Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 108-118
  • November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lachitatu, November 1
  • Lachinayi, November 2
  • Lachisanu, November 3
  • Loweruka, November 4
  • Lamlungu, November 5
  • Lolemba, November 6
  • Lachiwiri, November 7
  • Lachitatu, November 8
  • Lachinayi, November 9
  • Lachisanu, November 10
  • Loweruka, November 11
  • Lamlungu, November 12
  • Lolemba, November 13
  • Lachiwiri, November 14
  • Lachitatu, November 15
  • Lachinayi, November 16
  • Lachisanu, November 17
  • Loweruka, November 18
  • Lamlungu, November 19
  • Lolemba, November 20
  • Lachiwiri, November 21
  • Lachitatu, November 22
  • Lachinayi, November 23
  • Lachisanu, November 24
  • Loweruka, November 25
  • Lamlungu, November 26
  • Lolemba, November 27
  • Lachiwiri, November 28
  • Lachitatu, November 29
  • Lachinayi, November 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 108-118

November

Lachitatu, November 1

Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutira.​—Gen. 25:8.

Mawu akuti Abulahamu anakhala ndi moyo “wautali ndi wokhutira,” sakutanthauza kuti sankafunanso kukhala ndi moyo. Baibulo limati Abulahamu ankayembekezera “mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:10) Abulahamu ayenera kuti adzasangalala kwambiri kukhala m’Paradaiso padzikoli n’kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. Adzasangalalanso akadzadziwa kuti chitsanzo chake chathandiza anthu a Yehova kwa zaka zambirimbiri. Komanso adzadziwa kuti zimene Yehova anamuuza zoti apereke nsembe Isaki, zinkaimira zinthu zina zofunika kwambiri. (Aheb. 11:19) Adzadziwanso kuti chisoni chimene anamva pamene ankakonzekera kupereka nsembe Isaki, chinathandiza anthu kumvetsa mmene Yehova anamvera pamene anapereka nsembe Mwana wake Yesu.​—Yoh. 3:16. w16.02 1:15, 16

Lachinayi, November 2

Chimwana cha mkazi wopanduka iwe. Ukuganiza sindikudziwa kuti wasankha kugwirizana ndi mwana wa Jese, ndi kudzichititsa wekha manyazi ndiponso kuvula mayi ako?​—1 Sam. 20:30.

Zimakhala zovuta kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ngati m’bale waudindo watiganizira molakwika. Yonatani anakumananso ndi vuto ngati limeneli. Mfumu Sauli, yemwe anali wodzozedwa wa Yehova, ankadziwa kuti Yonatani ankagwirizana kwambiri ndi Davide koma sankadziwa chifukwa chake. Choncho pa nthawi ina, Sauli anakwiya kwambiri ndipo anachititsa manyazi Yonatani pa maso pa anthu. Koma Yonatani sanabwezere. Iye anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu komanso kwa Davide yemwe kenako anakhala mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 20:31-41) Abale amene akutsogolera mumpingo amayesetsa kuchitira aliyense zinthu zachilungamo. Komabe popeza anthuwa si angwiro, nthawi zina angatichitire kapena kutiganizira molakwa. (1 Sam. 1:13-17) Zoterezi zikachitika, tiziyesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. w16.02 3:14, 15

Lachisanu, November 3

Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo.​—Mat. 16:24.

Anthu ena satha kusiyanitsa pakati pa kudzipereka ndi kubatizidwa. Mwachitsanzo, achinyamata ena amati anadzipereka kwa Yehova koma sanakonzeke kuti abatizidwe. Kodi zimenezi n’zomveka? Ayi, chifukwa munthu akadzipereka kwa Yehova ndiye kuti wamulonjeza kuti akufuna kumutumikira moyo wake wonse. Ndiyeno pamene akubatizidwa amakhala akuuza anthu onse kuti anapemphera kwa Yehova ndipo anamulonjeza kuti wadzipereka kwa iye. Choncho ubatizo umathandiza anthu kudziwa kuti munthuyo anadzipereka. Koma munthu aliyense asanabatizidwe amafunika kumvetsa kuti kudzipereka kumatanthauza chiyani. Mwachidule tingati, munthu akadzipereka kwa Yehova amakhala kuti wasankha zoti azichita zofuna za Yehovayo osati zake. Amalonjeza kuti aziyesetsa kuti zinthu zina zisamamulepheretse kuchita zimene Yehova amafuna. Munthu akalonjeza zinazake amafunika kukwaniritsa. Choncho tiyenera kukwaniritsa zimene tinalonjeza kwa Yehova.​—Mat. 5:33. w16.03 1:14, 15

Loweruka, November 4

Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi.​—Aef. 4:15.

Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha thupi la munthu pofotokoza kuti Mkhristu aliyense angathandize kuti mpingo ukhale wogwirizana komanso kuti uzitsatira Yesu yemwe ndi Mutu wa mpingo. Mtumwiyu ananena kuti malo amene mafupa amalumikizana ndi amene amathandiza kuti thupi likhale logwirizana. (Aef. 4:16) Ndiye kodi tingatani kuti mpingo wathu uzigwirizana komanso uziyenda bwino? Tiyenera kulemekeza akulu amene Yesu wawaika mumpingo komanso kutsatira malangizo awo. (Aheb. 13:7, 17) Nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Komabe tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti uzitithandiza kumvera akulu ndi mtima wonse. Tizidziwa kuti tikamamvera modzichepetsa malangizo a akulu, zimathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana komanso kuti tizikondana kwambiri ndi Akhristu anzathu. w16.03 3:8, 9

Lamlungu, November 5

Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.​—Aheb. 4:12.

Achinyamata ambiri salimbikitsidwa kuti adzatumikire Yehova akadzakula. Achinyamatawa sanaphunzitsidwe kuika Yehova pamalo oyamba adakali aang’ono. (Mat. 10:24) Choncho mkulu amafunika kupeza mpata wocheza ndi wachinyamata amene akufuna kumuthandizayo. Ayeneranso kumuthandiza kudziwa kuti ndi wofunika kwambiri mumpingo. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono mkuluyo ayenera kukambirana naye malemba amene angamuthandize kuganizira zimene analonjeza podzipereka kwa Yehova. (Mlal. 5:4; Yes. 6:8; Mat. 6:24, 33; Luka 9:57-62; 1 Akor. 15:58; 2 Akor. 5:15; 13:5) Mwina angamufunse kuti, ‘Kodi pamene unkadzipereka kwa Yehova unamulonjeza kuti chiyani?’ Kenako angamufunse kuti, ‘Ukuganiza kuti Yehova anamva bwanji tsiku limene unabatizidwa?’ (Miy. 27:11) ‘Nanga ukuganiza kuti Satana anamva bwanji?’ (1 Pet. 5:8) Akulu ayenera kukumbukira kuti ngati atawerenga malemba oyenerera, akhoza kuthandiza achinyamata kusintha kwambiri. w15 4/15 2:9, 11

Lolemba, November 6

Muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.​—1 Pet. 5:7.

N’chifukwa chiyani nthawi zina mapemphero ena sayankhidwa nthawi yomweyo? Choyamba tiyenera kukumbukira kuti Yehova ali ngati bambo athu. (Sal. 103:13) Kodi ana ayenera kuyembekezera kuti bambo awo aziwapatsa chilichonse chimene apempha pa nthawi yomweyo? Nthawi zina ana amangopempha zinthu zosafunika kwenikweni zimene angozilakalaka pa nthawiyo. Ndiye pali zinthu zina zimene amapempha zomwe ayenera kudikira kaye. Koma amatha kupemphanso zinthu zimene sizingathandize iwowo kapena anthu ena. Ndipotu bambo atati azingopereka chilichonse kwa mwana, zikhoza kukhala ngati mwanayo ndi bwana ndipo bambowo ndi wantchito. Choncho m’pomveka kuti nthawi zina Yehova sayankha mapemphero athu nthawi yomweyo. Yehova ali ndi ufulu wochita zimenezi chifukwa chakuti iye ndi Atate wathu wachikondi komanso amene anatilenga. Atati azingopereka chilichonse pa nthawi imene tapempha ndiye kuti sangakhale ndi ufulu umene bambo kapena Mlengi amayenera kukhala nawo.​—Yes. 29:16; 45:9. w15 4/15 4:6, 7

Lachiwiri, November 7

Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.​—Yak. 4:7.

Pamene tikuyandikira kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiriza, Satana akufuna kuti tipuse, tiyambe ‘kudzikomera mtima’ ndiponso tiiwale zoti tili m’masiku otsiriza. Choncho “khalanibe maso” ndipo musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. (Mat. 16:22, 23; 24:42) Tisayerekeze ngakhale pang’ono kukhulupirira mabodza a Satana oti mapeto ali kutali kapena safika. Satana amafuna kuti tiziganiza kuti Mulungu satikonda ndipo sangatikhululukire machimo athu. Koma limeneli ndi bodza lankunkhuniza. Satanayo ndi amene sangakondedwe kapena kukhululukiridwa ndi Yehova. Koma Baibulo limanena kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Yehova amasangalala tikamayesetsa kumutumikira ndipo sadzaiwala zimene tikuchita. (1 Akor. 15:58) Tiyeni tisalole kuti Satana atipusitse. w15 5/15 1:16-19

Lachitatu, November 8

Anawaona ali patali ndi kuwalandira.​—Aheb. 11:13.

Abulahamu ankatumikira Mulungu mwakhama chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri malonjezo ake. Chikhulupirirochi chinamuthandiza kuchoka mumzinda wa Uri ndiponso kuti asakhazikike m’mizinda ya Kanani. Maziko a mizinda yonseyi anali osalimba chifukwa olamulira ake anali osaopa Mulungu. (Yos. 24:2) Abulahamu “anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:10) Abulahamu ankaona m’maganizo mwake ali mumzinda wolamulidwa ndi Yehova. Abele, Inoki, Nowa, Abulahamu ndi atumiki ena a Yehova ankakhulupirira kuti akufa adzauka. Iwo ankayembekezera Ufumu wa Mulungu womwe ndi “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” Kuganizira zinthu zimenezi kunawathandiza kukhulupirira kwambiri Yehova.​—Aheb. 11:15, 16. w15 5/15 3:8, 9

Lachinayi, November 9

Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu.​—1 Akor. 1:24.

Zinthu zodabwitsa zimene Yesu ankachita zinkasonyeza mphamvu za Yehova. Mabuku 4 a Uthenga Wabwino amafotokoza zinthu ngati zimenezi ndipo kuziwerenga kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Koma n’kutheka kuti Yesu anachita zozizwitsa zina zambiri zimene sizinalembedwe. (Mat. 9:35; Luka 9:11) M’pomveka kuti mtumwi Paulo ananena kuti: “Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu.” Koma kodi tikuphunzira chiyani pa zinthu zodabwitsa zimene Yesu ankachita? Mtumwi Petulo ananenanso kuti Yesu ankachita “zodabwitsa.” (Mac. 2:22) Zomwe Yesu ankachita zimasonyeza zinthu zosangalatsa zimene adzachite padziko lonse akamadzalamulira. Zimatithandizanso kudziwa bwino makhalidwe ake ndiponso a Atate wake. w15 6/15 1:1, 2

Lachisanu, November 10

Mumtima mwake anali kunena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”​—Maliko 5:28.

Yesu anazindikira kuti Yehova ndi amene wachiritsa mayi amene anagwira malaya ake ndipo anamulankhula mwachifundo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.” Satana amafuna kuti tiziganiza zoti ndife osafunika ndipo palibe amene amatikonda. Koma Yesu amakonda kwambiri anthu ndipo amamvera chisoni amene akudwala. (Maliko 5:34) Zozizwitsa zake zimatitsimikizira zimenezi. Apa n’zoonekeratu kuti tili ndi Mfumu ndiponso Mkulu wa Ansembe wachifundo kwambiri. (Aheb. 4:15) N’zovuta kumvetsa bwinobwino anthu amene akhala akudwala kwa nthawi yaitali ngati ifeyo sitinadwalepo choncho. Koma tizikumbukira kuti Yesu ankamvera chifundo anthu odwala ngakhale kuti iye sanadwalepo. Choncho tiyeni tiziyesetsa kutsatira chitsanzo chake.​—1 Pet. 3:8. w15 6/15 2:11, 12

Loweruka, November 11

Dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu chifukwa cha inu.​—Aroma 2:24.

Ifeyo tili ndi mwayi wodziwa dzina la Mulungu komanso wokhala “anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14; Yes. 43:10) Timapempha Yehova kuti dzina lake liyeretsedwe. (Mat. 6:9) Koma tiyenera kumupemphanso kuti azitithandiza kupewa chilichonse chimene chinganyozetse dzinalo. Sitifuna kufanana ndi anthu ena a m’nthawi ya atumwi amene zochita zawo zinkasemphana ndi zimene ankalalikira, monga mmene taonera mulemba laleroli. Kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, Yehova ayenera kuchotsa aliyense amene amakana ulamuliro wake. (Ezek. 38:22, 23) Kenako anthu onse adzathandizidwa kuti akhale angwiro. Timalakalaka kwambiri nthawi imene aliyense adzaganiza, kulankhula komanso kuchita zinthu zolemekeza dzina la Mulungu. Pamapeto pake, Atate wathu wakumwamba adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”​—1 Akor. 15:28. w15 6/15 4:7, 10

Lamlungu, November 12

Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu, ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.​—Yes. 66:1.

M’Malemba Achiheberi, mawu oti “chopondapo mapazi” amagwiritsidwanso ntchito pofotokoza za kachisi wa ku Yerusalemu. (1 Mbiri 28:2; Sal. 132:7) Popeza kachisiyu anali ngati likulu la kulambira koona, Yehova ankaona kuti ndi wokongola kwambiri. Tingati kachisiyo ankalemekeza malo oikapo mapazi a Yehova. (Yes. 60:13) Koma masiku ano padzikoli palibe kachisi weniweni amene tinganene kuti ndi likulu la kulambira koona. M’malomwake, pali kachisi wauzimu amene amalemekeza Yehova kuposa kachisi wina aliyense. Kachisi wauzimuyu akuimira zimene Mulungu akuchita pothandiza anthu kuti agwirizanenso naye komanso azimulambira. Izi zikutheka chifukwa cha nsembe ya Yesu komanso udindo wake monga Mkulu wa Ansembe. Kachisiyu anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E. pamene Yesu anabatizidwa. Pa nthawiyi, iye anadzozedwa kuti akhale Mkulu wa Ansembe m’kachisi wauzimu ameneyu.​—Aheb. 9:11, 12. w15 7/15 1:1-3

Lolemba, November 13

Adzaona Mwana wa munthu akubwera mumtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.​—Luka 21:27.

Imeneyi idzakhala nthawi yopereka mphoto kwa anthu okhulupirika komanso yolanga anthu osakhulupirika. (Mat. 24:46, 47, 50, 51; 25:19, 28-30) Malinga ndi zimene Mateyu analemba, Yesu anamaliza kufotokoza chizindikiro cha masiku otsiriza popereka fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Iye anati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.” (Mat. 25:31-33) Nangano n’chiyani chidzachitikire nkhosa ndi mbuzi? Anthu oipa, amene ali ngati mbuzi, “adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu.” Koma anthu olungama, omwe ali ngati nkhosa, adzalandira moyo wosatha.​—Mat. 25:46. w15 7/15 2:11, 12

Lachiwiri, November 14

Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!​—Sal. 133:1.

Mwachibadwa, anthufe timakonda kumene tinachokera, chilankhulo chathu kapena chakudya chimene tinazolowera. Koma tiyenera kupewa maganizo akuti zathuzo n’zabwino kuposa za ena. Yehova analenga zinthu zosiyanasiyana n’cholinga choti tizisangalala. (Sal. 104:24; Chiv. 4:11) Ndiye palibe chifukwa choganizira kuti zina ndi zabwino kapena zapamwamba kuposa zina. Yehova amafuna kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe choonadi molondola kuti adzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Tim. 2:3, 4) Kunena zoona, zimakhala zosangalatsa ngati tilolera maganizo osasemphana ndi mfundo za m’Baibulo amene anthu ena angakhale nawo. Izi zimathandizanso kuti tizigwirizana. Tiyeni tiziyesetsa kupewa mikangano ya m’dzikoli n’kumakhalabe okhulupirika kwa Yehova. Si bwino kulola kuti zinthu zina zitilekanitse. Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatithandiza kupewa maganizo a m’dziko la Satanali amene amachititsa anthu kukhala atsankho, onyada ndiponso okonda kupikisana. w15 7/15 3:17, 18

Lachitatu, November 15

[Mulungu] amakuderani nkhawa.​—1 Pet. 5:7.

Tingasonyeze kuti timakonda Yehova ndiponso anzathu tikamachita khama pa ntchito yolalikira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timasonyezanso kuti timakonda kwambiri Yehova tikamakhala okhulupirika poyesedwa. (Sal. 84:11; Yak. 1:2-5) Tikakumana ndi mavuto aakulu, tisakayikire kuti Mulungu amadziwa mmene tikumvera ndipo adzatithandiza. Tikutero chifukwa chakuti iye amaona kuti ndife amtengo wapatali. (Sal. 56:8) Timaganizira zimene Mulungu analenga ndiponso zochita zake chifukwa chomukonda kwambiri. Timasonyezanso kuti timakonda Mulungu ndiponso kuyamikira Mawu ake tikamaphunzira Baibulo mwakhama. Timapempheranso kwa Mulungu pafupipafupi chifukwa chomukonda. Kuganizira nsembe ya dipo imene Mulungu anapereka chifukwa cha machimo athu kumatithandizanso kumukonda kwambiri. (1 Yoh. 2:1, 2) Izi ndi zinthu zochepa chabe zimene Yehova watichitira zomwe zimatichititsa kumukonda kwambiri. w15 8/15 1:6, 17, 18

Lachinayi, November 16

[Ndi bwino kukhala] woleza mtima.​—Mlal. 7:8.

Mwina pa nthawi zina m’dziko latsopano tidzafunika kukhala oleza mtima. Mwachitsanzo, tikhoza kudzamva kuti anthu ena aukitsidwa ndipo achibale awo komanso anzawo akusangalala. Koma mwina ife tidzafunika kudikirabe kuti achibale athu aukitsidwe. Ndiye kodi tidzasangalala ndi anzathuwo n’kumadikira moleza mtima? (Aroma 12:15) Ngati panopa timayembekezera malonjezo a Yehova moleza mtima sitidzavutika kukhala oleza mtima pa nthawiyo. Komanso nthawi zina gulu la Yehova limasintha mmene limafotokozera mfundo zina za m’Baibulo. Kodi timaphunzira mfundozo mwakhama n’kumakhala oleza mtima ngakhale pamene sitikuzimvetsa bwino? Ngati timatero ndiye kuti sitidzavutika kukhala oleza mtima m’dziko latsopano pamene Yehova azidzatipatsa malangizo.​—Miy. 4:18; Yoh. 16:12. w15 8/15 3:9, 10

Lachisanu, November 17

Tidzafike . . . pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.​—Aef. 4:13.

Mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu a ku Efeso kuti awalimbikitse kuti ‘afike pa umodzi m’chikhulupiriro komanso pa kumudziwa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikira adzakhale achikulire, ofika pa msinkhu umene Khristu anafikapo.’ (Aef. 4:13) Pamene Paulo ankalemba kalatayi n’kuti patatha zaka zingapo kuchokera pamene mpingo wa ku Efeso unakhazikitsidwa. Anthu ambiri mumpingowu anali atafika pokhala Akhristu olimba. Koma ena ankafunikabe kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu. Ndi mmene zililinso ndi Mboni za Yehova masiku ano. Abale ndi alongo ambiri akhala akutumikira Mulungu kwa nthawi yaitali ndipo ndi Akhristu olimba. Koma pali ena amene sanafikebe pamenepo. Mwachitsanzo, chaka chilichonse anthu ambirimbiri amabatizidwa ndipo amafunika kupitiriza kukula mpaka kufika pokhala Akhristu olimba. Kodi inuyo muli m’gulu la anthu oterewa?​—Akol. 2:6, 7. w15 9/15 1:2, 3

Loweruka, November 18

Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.​—1 Tim. 4:8.

Anthu ambiri amaona kuti masewera amathandiza thupi komanso maganizo. Koma ngati tikufuna kuchita masewera pagulu, tiyenera kusamala ndi anthu amene timachita nawo masewerawo. Paja lemba la Miyambo 13:20 limanena kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Choncho chikumbumtima chathu chiyenera kutithandiza kusankha bwino anthu amene tingamachite nawo zosangalatsa. Posankha zosangalatsa tiyenera kuganiziranso nthawi. Kodi chimene mumaika patsogolo n’chiyani? Kodi nthawi zambiri mumalephera kusonkhana, kulalikira ndiponso kuphunzira panokha chifukwa cha zosangalatsa? Paja Yesu anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mat. 6:33) Kodi chikumbumtima chanu chimakuthandizani kuti muzitsatira malangizo a Yesuwa? w15 9/15 2:13, 15

Lamlungu, November 19

N’chifukwa chiyani wapsa mtima choncho, ndipo nkhope yako yagweranji? Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? . . . Kodi iweyo suugonjetsa [uchimo]?​—Gen. 4:6, 7.

Amenewa anali malangizo othandiza kwambiri. Yehova anapatsa Kaini malangizowa ataona kuti Kainiyo watsala pang’ono kuchita zoipa. Koma Kaini sanamvere ndipo zotsatira zake zinali zoipa kwambiri. (Gen. 4:11-13) Pa nthawi ina, mlembi wa Yeremiya dzina lake Baruki, anakhumudwa kwambiri ndipo Yehova anamuthandiza kuzindikira vuto lake lenileni. Koma mosiyana ndi Kaini, Baruki anamvera malangizo a Yehova ndipo anapulumuka. (Yer. 45:2-5) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamulandira monga mwana wake.” (Aheb. 12:6) Palembali, mawu akuti ‘kulanga’ amatanthauzanso kuphunzitsa m’njira zosiyanasiyana. M’Baibulo muli zitsanzo zosonyeza kuti Yehova ankalola kuti atumiki ake ena akumane ndi mavuto pofuna kuwathandiza kukhala anthu abwino. w15 9/15 4:12, 13

Lolemba, November 20

Akapolo anufe . . . tabwera chifukwa tamva za dzina la Mulungu wanu, Yehova. Tamva mbiri yake ndi zonse zimene anachita.​—Yos. 9:9.

Anthu a ku Gibeoni anazindikira kuti Mulungu woona ndi amene akuthandiza Aisiraeli. Nayenso Rahabi anazindikira kuti Mulungu ankathandiza Aisiraeli. Iye anamva mmene Yehova anawapulumutsira, ndipo amuna awiri atabwera kudzazonda mzinda wa Yeriko, anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.” Rahabi analolera kuika moyo wake pa ngozi podziwa kuti Yehova akhoza kumupulumutsa limodzi ndi banja lake. (Yos. 2:9-13; 4:23, 24) Zitsanzo za m’Baibulo ngati zimenezi zikutithandiza kumvetsa tanthauzo la kuona Mulungu komanso kuzindikira mphamvu za dzanja lake. Tikayamba kudziwa bwino Yehova timamvetsa makhalidwe ake komanso zochita zake ndipo zimakhala ngati tikumuona komanso tikuona dzanja lake. (Aef. 1:18) Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala ngati anthu akale komanso a masiku ano amene amazindikira mphamvu za dzanja la Yehova. w15 10/15 1:6, 7, 9

Lachiwiri, November 21

Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.​—Yoh. 11:5.

Baibulo limanena kuti Yesu ankakonda Marita. Koma sikuti ndi Marita yekha amene Yesu ankagwirizana naye. Yesu ankakonda ndiponso kulemekeza azimayi ena monga amayi ake komanso Mariya yemwe anali mchemwali wake wa Marita. (Yoh.19:25-27) Koma kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankakonda kwambiri Marita? Chifukwa chakuti Marita ankalandira bwino alendo, anali wakhama komanso ankakonda kwambiri Mulungu. Marita ankakhulupirira kwambiri zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo sankakayikira kuti Yesu ndi Mesiya wolonjezedwa. (Yoh. 11:21-27) Koma Marita sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Mwachitsanzo, tsiku lina Yesu atapita kunyumba kwawo, iye anakhumudwa ndi zimene Mariya anachita ndipo anauza Yesu kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekerera ndekha ntchito? Tamuuzani kuti andithandize.”​—Luka 10:38-42. w15 10/15 3:1, 2

Lachitatu, November 22

Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.​—Yak. 4:8.

Kuganizira za Yehova ndi Yesu kumatithandiza kuti tisafooke. Tikatero timalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo komanso anthu amene timawapeza tikamalalikira. Kuganizira kwambiri zimene Yehova anachita popereka dipo kungatithandizenso kuti tiziona kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wofunika kwambiri. (Aroma 3:24) M’bale wina wa ku South Africa dzina lake Mark anakhala m’ndende kwa zaka zitatu chifukwa chokana usilikali ndipo anati: “Munthu akamasinkhasinkha zimakhala ngati akuyenda ulendo n’kumaona zinthu zatsopano. Zili choncho chifukwa chakuti akamaganizira amazindikira zinthu zatsopano zokhudza Yehova. Nthawi zina ndimada nkhawa ndikaganizira za m’tsogolo. Koma ndikangotenga Baibulo n’kuwerenga nkhani inayake, mtima wanga umakhala m’malo.” w15 10/15 4:15

Lachinayi, November 23

Ndithandizeni kukhala wozindikira kuti nditsatire chilamulo chanu, ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wonse.​—Sal. 119:34.

Ngati n’zotheka, muziwauza ana anu achinyamata chifukwa chimene chakuchititsani kusankha zinazake kapena kupereka lamulo linalake. Ana anu akamvetsa chifukwacho, sizingawavute kumvera. M’bale wina dzina lake Barry ali ndi ana 4 ndipo anati: “Kufotokoza zifukwa kumathandiza kuti ana anu azikudalirani chifukwa amaona kuti mumapereka malamulo muli ndi zifukwa zomveka.” Tizikumbukira kuti mosiyana ndi ana aang’ono, achinyamata amayamba kuganiza kwambiri ndiponso kusankha okha zochita. (Aroma 12:1) A Barry ananenanso kuti: “Achinyamata ayenera kuphunzira kusankha zinthu ataganizira kaye osati mopupuluma.” Choncho muzidzichepetsa n’kumauza ana anu achinyamata chifukwa chimene mwasankhira zinazake. Zimenezi zingawathandize kuti azisankha zochita mwanzeru ndiponso kuona kuti simuwaderera. w15 11/15 2:11

Lachisanu, November 24

Tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.​—Agal. 6:10.

Padziko lapansi pali Akhristu anzathu ambiri amene amalambiranso Yehova. Ndiye kodi tiziwaona bwanji? (Aroma 12:10) Mtumwi Petulo analemba kuti: “Tsopano, popeza mwayeretsa miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo, kondanani kwambiri kuchokera mumtima.” Iye anauzanso Akhristu anzake kuti: “Koposa zonse, khalani okondana kwambiri.” (1 Pet. 1:22; 4:8) Gulu lathu lapadziko lonse ndi lapadera kwambiri chifukwa chakuti timakondana. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyera chifukwa choti timamukonda ndiponso timamvera malamulo ake. Mzimuwo ndi wamphamvu kwambiri ndipo umatithandiza kukhala ogwirizana ndi abale ndi alongo athu padziko lonse.​—1 Yoh. 4:20, 21. w15 11/15 4:8, 9

Loweruka, November 25

Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse . . . [adzanena] kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi.”​—Zek. 8:23.

Yehova satikakamiza kuphunzira chilankhulo chinachake kuti timudziwe ndiponso kumvetsa zimene amafuna. (Chiv. 7:9, 10) Iye salephera kulankhula ndi anthu chifukwa choti anthuwo amalankhula zilankhulo zosiyanasiyana. N’zoona kuti m’Baibulo muli mawu ochepa a chilankhulo chimene Yesu ankalankhula akamaphunzitsa anthu. (Mat. 27:46; Maliko 5:41; 7:34; 14:36) Komabe Yehova anaonetsetsa kuti zimene Yesu anaphunzitsa zimasuliridwe m’Chigiriki ndiponso m’zilankhulo zina. Ayuda ndiponso Akhristu ankakopera Malemba ndipo izi zinathandiza kuti Malembawo asungike. Ndiyeno zimene anakoperazo zinamasuliridwa m’zilankhulo zina. Pafupifupi zaka 400 kuchokera pamene Yesu anaphedwa, mtsogoleri wina wachipembedzo ananena kuti zimene Yesu anaphunzitsa zinali zitamasuliridwa m’zilankhulo zambiri. Mwachitsanzo, zinali zitamasuliridwa m’chilankhulo cha ku Siriya, Iguputo, Indiya, Perisiya komanso ku Itiyopiya. w15 12/15 1:10, 11

Lamlungu, November 26

Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.​—Miy. 15:23.

Zimene tikufuna kunena zikhoza kukhala zolimbikitsa, komabe ngati sitinazilankhule pa nthawi yoyenera sizingathandize. Mwachitsanzo mu March 2011, ku Japan kunachitika chivomerezi komanso kunasefukira madzi ndipo mizinda yambiri inawonongeka. Anthu oposa 15,000 anafa. Ngakhale kuti abale ndi alongo akuderali nawonso anakhudzidwa ndi vutoli, anayesetsa kulimbikitsa anzawo pogwiritsa ntchito Baibulo. Komabe anthu ambiri akumeneko ndi achipembedzo chachibuda moti sadziwa mfundo za m’Baibulo ndipo amakhulupirira zosiyana kwambiri ndi zimene limaphunzitsa. Choncho abale anadziwa kuti nthawiyi sinali yabwino kuti auze anthu amene anaferedwa zoti Mulungu adzaukitsa akufa. M’malomwake anangowalimbikitsa n’kuwauza kuchokera m’Baibulo chifukwa chake anthu abwino nawonso amakumana ndi mavuto. w15 12/15 3:7

Lolemba, November 27

Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.​—Miy. 14:15.

Tikadwala, anthu ambiri m’dziko loipali amapezerapo mwayi wochita bizinezi. Ndipo anthu kapena makampani ena amalimbikitsa kwambiri anthu kugwiritsa ntchito mankhwala komanso zinthu zina zodula n’cholinga chongofuna kupeza ndalama zambiri. Munthu amene akuvutika kwambiri ndi matenda angatengeke mosavuta ndi zimenezi. Koma “munthu wochenjera” samangokhulupirira zilizonse zimene anthu osadziwa kwenikweni za mankhwala anganene. M’malomwake angadzifunse kuti: ‘Akuti mankhwalawa anathandizapo munthu wina, koma kodi pali umboni uliwonse woti zimenezi ndi zoona? Ngakhale zitakhala kuti ndi zoona, kodi mankhwala amenewa angandithandizenso ineyo? Nanga kodi pangafunike kuti ndifufuze kaye, mwinanso ndifunse dokotala kapena munthu wina wodziwa bwino za matenda angawa?’​—Deut. 17:6. w15 12/15 4:14, 15

Lachiwiri, November 28

Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza.​—2 Akor. 5:14.

Paulo ankadziwa kuti munthu akamayamikira chikondi chimene Yesu anasonyeza, amayamba kukonda kwambiri Yesuyo. Tikamaganizira ndi kumvetsa bwino zimene Yehova anatichitira, timayamikira kwambiri chikondi chake. Komanso timafunitsitsa kukhala ndi moyo wogwirizana ndi zimene Yesu amafuna. Koma kodi tingasonyeze bwanji zimenezi? Popeza timakonda Yehova, timayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu mosamala kwambiri komanso kuchita zimene Mulungu ndi Khristu amafuna. (1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 2:6) Yesu anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda.” (Yoh. 14:21; 1 Yoh. 5:3) Ndiye tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene ndimachita bwino potsanzira Yesu? Nanga ndi zinthu ziti zimene ndiyenera kusintha?’ Tiyenera kudzifunsa mafunso amenewa chifukwa nthawi zonse timakakamizidwa kutsatira zimene anthu a m’dzikoli amachita.​—Aroma 12:2. w16.01 2:7-9

Lachitatu, November 29

Tidzakhala ngati iyeyo, chifukwa tidzamuona mmene alili.​—1 Yoh. 3:2.

Kodi mukuona kuti mumalalikira mwakhama? Nanga mumakonda kwambiri kuphunzira Baibulo kuti mudziwe “zinthu zozama za Mulungu”? (1 Akor. 2:10) Kodi mukuona kuti Yehova akukudalitsani kwambiri pa ntchito yolalikira? Kodi mumafunitsitsa kuchita zimene Yehova amafuna? Nanga kodi mumafunitsitsanso kuthandiza ena kuti ayambe kutumikira Yehova? Kodi nthawi zina mumaona kuti Yehova amakuthandizani m’njira yodabwitsa? Ngati yankho lanu pa mafunso onsewa ndi lakuti inde, kodi ndiye kuti ndinu wodzozedwa? Ayi. Tikutero chifukwa choti si odzozedwa okha amene angayankhe kuti inde pa mafunsowa. Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake kuthandiza Akhristu onse, kaya ndi opita kumwamba kapena odzakhala padzikoli. Ndipotu ngati mumakayikira zoti mwina ndinu wodzozedwa, ndiye kuti si inu wodzozedwa. w16.01 3:14, 15

Lachinayi, November 30

Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.​—Miy. 8:30.

Yesu akamagwira ntchito ndi Atate wake ankasangalala ndi ntchitoyo komanso chifukwa chodziwa kuti Atatewo amamukonda. Ifenso tikamagwira ntchito ndi Mulungu timasangalala. Yesu ananena kuti munthu amasangalala akapatsidwa zinthu komanso akapatsa ena zinthu. (Mac. 20:35) Choncho pamene munthu wina anatiphunzitsa mfundo za m’Baibulo tinasangalala kwambiri. Timasangalalanso tikamauza ena zimene tinaphunzirazo. Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, ena amasangalala kwambiri chifukwa amayamba kudziwa Mulungu ndiponso kumvetsa mfundo za m’Mawu ake. Ifenso timasangalala kuona kuti anthuwo akusintha mmene amaganizira komanso zochita zawo. Izi zimatithandiza kuzindikira kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Ntchitoyi imathandiza anthu kuti agwirizanenso ndi Mulungu ndiponso kuti adzapeze moyo wosatha. (2 Akor. 5:20) Choncho palibe ntchito yosangalatsa kwambiri kuposa yolalikira. w16.01 5:6, 7

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena