Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 118-128
  • December

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lachisanu, December 1
  • Loweruka, December 2
  • Lamlungu, December 3
  • Lolemba, December 4
  • Lachiwiri, December 5
  • Lachitatu, December 6
  • Lachinayi, December 7
  • Lachisanu, December 8
  • Loweruka, December 9
  • Lamlungu, December 10
  • Lolemba, December 11
  • Lachiwiri, December 12
  • Lachitatu, December 13
  • Lachinayi, December 14
  • Lachisanu, December 15
  • Loweruka, December 16
  • Lamlungu, December 17
  • Lolemba, December 18
  • Lachiwiri, December 19
  • Lachitatu, December 20
  • Lachinayi, December 21
  • Lachisanu, December 22
  • Loweruka, December 23
  • Lamlungu, December 24
  • Lolemba, December 25
  • Lachiwiri, December 26
  • Lachitatu, December 27
  • Lachinayi, December 28
  • Lachisanu, December 29
  • Loweruka, December 30
  • Lamlungu, December 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 118-128

December

Lachisanu, December 1

Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.​—Sal. 25:14.

Baibulo limasonyeza maulendo atatu kuti Abulahamu anali bwenzi la Mulungu. (2 Mbiri 20:7; Yes. 41:8; Yak. 2:23) Ndipotu m’Baibulo ndi Abulahamu yekha amene amatchedwa bwenzi la Mulungu. Koma kodi izi zikutanthauza kuti Abulahamu yekha ndi amene anali bwenzi la Yehova? Ayi. Baibulo limasonyeza kuti tonsefe tikhoza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. M’Mawu a Mulungu muli nkhani zambiri zokhudza amuna ndi akazi amene ankakhulupirira kwambiri Yehova. (Sal. 25:14) Mtumwi Paulo analemba kuti anthu amenewa ali m’gulu la “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Anthu onsewa anali ndi makhalidwe abwino osiyanasiyana ndipo anali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Tiyeni tiziyesetsa kutsanzira chikhulupiriro chawo. (Aheb. 6:11, 12) Tikatero tidzadalitsidwa kwambiri chifukwa tidzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova mpaka kalekale. w16.02 2:1, 2, 19

Loweruka, December 2

Ndinatsika . . . kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.​—Yoh. 6:38.

Tiyerekeze kuti munthu wakugulirani galimoto. Ndiyeno akukupatsani mapepala osonyeza kuti galimotoyo ndi yanu koma akukuuzani kuti: “Makiyi ndizisunga ndine ndipo ndiziyendetsanso galimotoyi ndi ineyo.” Kodi mungaganize kuti wakupatsanidi galimotoyo ndi mtima wonse? Nanga mukuganiza kuti Mulungu amayembekezera chiyani kwa munthu amene anadzipereka? Ndipo angamve bwanji ngati munthuyo atayamba moyo wachiphamaso, mwina kuchita chibwenzi ndi munthu woti si Mboni? Nanga bwanji ngati munthuyo atayamba ntchito yomwe ikumulepheretsa kulalikira ndi kusonkhana? Kodi zimenezi sizingafanane ndi kugulira munthu galimoto n’kukana kumupatsa makiyi? Paja munthu akadzipereka amakhala atauza Yehova kuti: “Ndikupereka moyo wanga kwa inu, ndipo tsopano ndine wanu. Ndimaona kuti zofuna zanu ndi zofunika kwambiri kuposa zanga ndipo ndiziyesetsa kuchita zofuna zanuzo.” Maganizo amenewa ndi ofanana ndi amene Yesu anali nawo, omwe ali mulemba laleroli. w16.03 1:16, 17

Lamlungu, December 3

Sindikusiyani.​—2 Maf. 2:2.

Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, mneneri Eliya anapempha Elisa kuti akhale mtumiki wake. Nthawi yomweyo iye anavomera ndipo anali wokhulupirika. Ankatumikira Eliya ngakhale pa ntchito zooneka ngati zonyozeka. (2 Maf. 3:11) Ndiyeno patapita zaka 6, Elisa anazindikira kuti kwatsala nthawi yochepa kuti Eliya asiye kutumikira ku Isiraeli. Pa nthawiyi Eliya anali ataphunzitsa Elisa zinthu zambiri ndipo anamuuza kuti asiye kumutsatira. Koma Elisa sanafune kusiyana ndi Eliya ngakhale pang’ono. Ngati ndinu m’bale wachinyamata, kodi mungatsanzire bwanji Elisa? Mukapatsidwa ntchito, ngakhale yooneka ngati yonyozeka, muziigwira mokhulupirika. Muziona kuti akulu amene akupatsani ntchitoyo ndi anzanu ndipo muzisonyeza kuti mukuyamikira kwambiri zimene akuchita pokuthandizani. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala okhulupirika? Mukakhala okhulupirika akulu adzaona kuti Yehova akufuna kuti mupatsidwe maudindo ena mumpingo.​—Sal. 101:6; 2 Tim. 2:2. w15 4/15 2:13, 14

Lolemba, December 4

Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.​—Sal. 15:4.

Sauli ankauza Yonatani kuti achite zinthu zimene zikanapangitsa kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 20:31) Koma Yonatani anali wokhulupirika kwa Mulungu ndipo anapitiriza kugwirizana ndi Davide m’malo molakalaka kuti adzakhale mfumu. Iye sanasinthe zimene analonjezana ndi Davide. Mwachitsanzo, ngati tinagwirizana zinazake pa nkhani za bizinezi, tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu poyesetsa kukwaniritsa zomwe tinagwirizanazo. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale pamene zinthu sizikuyenda mmene tinkaganizira. Nanga kodi tingatani ngati banja lathu silikuyenda bwino ngati mmene tinkayembekezera? Ngati timakondadi Mulungu, tidzayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa mnzathuyo. (Mal. 2:13-16) Komanso tizikhalabe okhulupirika kwa anthu a Mulungu, ngakhale atatikhumudwitsa. Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yehova. (Miy. 27:11) Ndipotu tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova, adzatidalitsa ndipo zinthu zidzatiyendera bwino. w16.02 3:16, 17

Lachiwiri, December 5

Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezera.​—Yes. 30:18.

Yehova amadziwa bwino zimene sitingakwanitse kuchita. (Sal. 103:14) Amadziwa kuti sitingapirire mavuto patokha ndipo ndiwokonzeka kutithandiza. N’zoona kuti nthawi zina timaona kuti sitingapirire. Koma Yehova amatitsimikizira kuti sangalole kuti atumiki ake ayesedwe kufika pamene sangapirire. Ndithu “iye adzapereka njira yopulumukira.” (1 Akor. 10:13) Choncho tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira kuti Yehova amadziwa bwino mavuto amene tingathe kuwapirira ndiponso amene sitingathe kuwapirira. Tiziyembekezera Yehova ngati tikuona kuti mapemphero athu sakuyankhidwa, chifukwa iye amadziwa nthawi imene angatithandize. Tiyeneranso kudziwa kuti iye amafunitsitsa kutithandiza koma amaleza mtima podikira nthawi yake. Paja Baibulo limati: “Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo.” w15 4/15 4:8, 9

Lachitatu, December 6

Ndi mmenenso kale akazi oyera amene anali kuyembekeza Mulungu anali kudzikongoletsera. Analinso kugonjera amuna awo.​—1 Pet. 3:5.

Ambiri amaona kuti kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse kumawathandiza. Pa nthawiyi, angakonzekere zoti akanene mu utumiki ndipo izi zingawathandize kuti azilalikira mogwira mtima. Aliyense akamafotokoza mfundo za m’Mawu a Mulungu n’kumasonyeza kuti amakonda Yehova ndipo akufuna kumutumikira, banja lonse limakhala logwirizana. Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi wake azigwirizana kwambiri. Iwo akamakonda kwambiri Yehova n’kumamutumikira, amakhala osangalala komanso ogwirizana. Abulahamu ndi Sara, Isaki ndi Rabeka komanso Elikana ndi Hana ankakondana kwabasi. (Gen. 26:8; 1 Sam. 1:5, 8) Inunso yesetsani kuti muzikondana kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Mukamachita zimenezi, mumakhala ogwirizana komanso ubwenzi wanu ndi Yehova umalimba.​—Mlal. 4:12. w16.03 3:12, 13

Lachinayi, December 7

Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye [Satana].​—1 Pet. 5:9.

Satana akulimbana kwambiri ndi odzozedwa amene ali padzikoli ndiponso a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Popeza wangotsala ndi kanthawi kochepa, Mdyerekezi akufuna kumeza atumiki ambiri a Yehova. (Chiv. 12:9, 12) Koma n’zotheka kugonjetsa Satana. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.” (Yak. 4:7) Anthu ambiri amanena kuti Satana kulibeko. Iwo amaganiza kuti Satana ndiponso ziwanda angokhala zinthu zotchulidwa m’mabuku, m’mafilimu ndiponso m’masewera a pakompyuta. Amanenanso kuti munthu wanzeru sangamakhulupirire zoti kuli ziwanda. Kodi mukuganiza kuti Satana amadandaula ndi zimene anthu amanenazi? Ayi ndithu. Ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti azipusitsa anthuwo mosavuta. (2 Akor. 4:4) Satana amapusitsa anthu ndi maganizo akuti iyeyo kulibeko ndiponso m’njira zina zosiyanasiyana. w15 5/15 2:1, 2

Lachisanu, December 8

[Mose] anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa kukhala chuma chochuluka kuposa chuma cha Iguputo, pakuti anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.​—Aheb. 11:26.

Zikuoneka kuti makolo ake a Mose anamuphunzitsa za Yehova komanso zoti Yehovayo ankafuna kulanditsa Aheberi ku ukapolo n’kupita nawo ku Dziko Lolonjezedwa. (Gen. 13:14, 15; Eks. 2:5-10) Kuganizira kwambiri malonjezo a Yehova kunachititsa Mose kumukonda kwambiri komanso kumukhulupirira ndi mtima wonse. M’pomveka kuti Mose ankakonda Yehova chifukwa Yehovayo anasonyeza kuti amamvera chisoni Aheberi komanso anthu onse. Kukonda Mulungu komanso kumukhulupirira kunathandiza Mose pa moyo wake wonse. (Deut. 6:4, 5) Mofanana ndi atumiki a Mulungu ena, nayenso ayenera kuti ankaganizira nthawi imene Yehova adzathetse imfa. (Yobu 14:14, 15; Aheb. 11:17-19) Pa nthawi ina, Farao anaopseza Mose kuti amupha koma iye sanachite mantha. Izi zinatheka chifukwa chakuti ankakhulupirira Mulungu, kumukonda ndiponso ankaona m’maganizo mwake zinthu zabwino zimene Mulungu analonjeza.​—Eks. 10:28, 29. w15 5/15 3:11-13

Loweruka, December 9

Vinyo waathera.​—Yoh. 2:3.

Yesu anachita chozizwitsa choyamba pa phwando la ukwati ku Kana m’dera la Galileya. Pa phwandoli, vinyo anatha mwina chifukwa chakuti kunabwera alendo ambiri kuposa amene ankayembekezera. Mayi ake a Yesu analiponso. Iwo ankadziwa kuti Yesu ndi “Mwana wa Wam’mwambamwamba” ndipo ayenera kuti kwa zaka zambiri ankaganizira maulosi onena za Yesuyo. (Luka 1:30-32; 2:52) Sitikudziwa ngati ankakhulupirira kuti Yesu ali ndi mphamvu zapadera zothandizira banjalo. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti pa phwandolo, Mariya ndi Yesu anamvera chisoni banja latsopanolo ndipo ankafuna kulithandiza kuti lisachite manyazi. Yesu ankadziwanso kuti kulandira bwino alendo n’kofunika kwambiri. Choncho anasandutsa madzi okwana malita 380 kukhala “vinyo wabwino.” (Yoh. 2:6) Sikuti Yesu ndi amene anali ndi udindo wopezera anthuwo vinyo. Koma ankaganizira kwambiri anthu ndipo ankatsanzira mtima wopatsa wa Atate wake. w15 6/15 1:3

Lamlungu, December 10

Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?​—Mac. 1:6.

Yesu asanapite kumwamba, ophunzira ake anamufunsa funso la mulemba la leroli. Zimene Yesu anayankha zinasonyeza kuti sinali nthawi yoti ophunzirawo adziwe pamene Ufumu wa Mulungu udzayambe kulamulira. Koma anawathandiza kuti aziganizira kwambiri ntchito yolalikira chifukwa inali yofunika kwambiri. (Mac. 1:7, 8) Komabe Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti aziyembekezera kubwera kwa Ufumu wa Mulungu. Kuyambira nthawi ya atumwi, Akhristu akhala akupemphera kuti Ufumuwu ubwere. Ndiyeno patapita zaka, Yehova anathandiza atumiki ake kudziwa nthawi imene Yesu adzayambe kulamulira kumwamba. Anachita zimenezi nthawiyo itatsala pang’ono kukwana. M’chaka cha 1876, Charles Taze Russell analemba nkhani yofotokoza zimenezi m’magazini ina. Nkhani yake inali yakuti: “Kodi Nthawi za Anthu a Mitundu Ina Zidzatha Liti?” Nkhaniyi inafotokoza kuti “nthawi zokwanira 7” zotchulidwa mu ulosi wa Danieli zikufanana ndi ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina’ zimene Yesu anatchula. Nkhaniyo inafotokozanso kuti nthawizi zidzatha mu 1914.​—Dan. 4:16; Luka 21:24. w15 6/15 4:11, 12

Lolemba, December 11

Yesu anagwetsa misozi.​—Yoh. 11:35.

Yesu ankamva chisoni kwambiri akaona anthu akuvutika. Mwachitsanzo, iye ataona anthu akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro, “anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.” Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti amuukitsa pasanapite nthawi yaitali. (Yohane 11:33-36) Yesu sanachite manyazi kulira pagulu. Kulira kwake kunathandiza anthu kudziwa kuti ankakonda kwambiri Lazaro ndi azichemwali ake. Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa poukitsa mnzakeyo. (Yoh. 11:43, 44) Baibulo limanena kuti Yesu ndi “chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo.” (Aheb. 1:3) Choncho, zozizwitsa za Yesu zimasonyeza kuti iye ndiponso Atate wake amafunitsitsa kuthetsa imfa komanso mavuto onse a anthu. Posachedwapa, Yehova ndi Yesu adzaukitsa anthu ambirimbiri. Paja Yesu ananena kuti “idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa.​—Yoh. 5:28, 29. w15 6/15 2:13, 14

Lachiwiri, December 12

Iwo atamande dzina lanu . . . lalikulu.​—Sal. 99:3.

Anthu a zipembedzo zina amakhulupirira kuti adzapita kumwamba ndipo amati adzatamanda Yehova akadzapita kumwambako. Koma ife timadziwa kuti tiyenera kumutamanda padzikoli ndipo nthawi yoti tiyambe ndi yomwe ino. Choncho timayesetsa kutsanzira atumiki a Yehova amene afotokozedwa pa Salimo 99:1-3, 5. Salimoli likusonyeza kuti Mose, Aroni ndi Samueli ankachita zonse zimene akanatha potumikira Mulungu. (Sal. 99:6, 7) Masiku anonso, pali Akhristu amene amatumikira Yehova mwakhama pabwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu. Ena amachita zimenezi podikira kupita kumwamba kukakhala ansembe limodzi ndi Yesu. Koma a “nkhosa zina” akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. (Yoh. 10:16) Ngakhale kuti maguluwa akuyembekezera zosiyana, onse amatumikira Yehova mogwirizana pamalo oikapo mapazi ake. Koma aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikuchita zimene ndingathe pothandiza kuti zinthu ziziyenda bwino m’gulu la Yehova?’ w15 7/15 1:4, 5

Lachitatu, December 13

Uziwayembekezerabe.​—Hab. 2:3.

Kwa nthawi yaitali, atumiki a Yehova akhala akuyembekezera kuti maulosi ena a m’Baibulo akwaniritsidwe. Yesaya, yemwe analosera kuti Yehova adzathandiza Ayuda kubwerera kwawo, anati: “Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezera.” (Yes. 30:18) Nayenso Mika analemba maulosi okhudza anthu a Mulungu ndipo anati: “Ndidzadikirira Yehova.” (Mika 7:7) Kwa zaka zambiri, atumiki a Mulungu ankayembekezeranso kukwaniritsidwa kwa maulosi okhudza Mesiya kapena kuti Khristu. (Luka 3:15; 1 Pet. 1:10-12) Masiku ano, palinso maulosi ena onena za Mesiya amene atumiki a Mulungu akuyembekezera. Posachedwapa Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya pothetsa mavuto onse a anthu. Adzachita zimenezi powononga anthu oipa ndiponso kupulumutsa anthu ake m’dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Choncho tiyenera kukhalabe maso chifukwa mapeto a dzikoli ali pafupi kwambiri. w15 8/15 2:1, 2

Lachinayi, December 14

Kudzipereka kwambiri panyumba yanu kudzandidya.​—Yoh. 2:17.

Yehova anauza Aisiraeli kuti amange chihema. (Eks. 25:8) Patapita nthawi, Aisiraeli anamanga kachisi kuti azilambiramo Yehova. (1 Maf. 8:27, 29) Ayuda atabwera ku ukapolo ku Babulo, ankasonkhana m’masunagoge. (Maliko 6:2; Yoh. 18:20; Mac. 15:21) Akhristu oyambirira ankasonkhana m’nyumba za anthu a mu mpingo. (Mac. 12:12; 1 Akor. 16:19) Masiku ano, Akhristu padziko lonse amalambira Yehova ndiponso kuphunzira Mawu ake m’Nyumba za Ufumu. Yesu ankakonda kwambiri kachisi wa Yehova wa ku Yerusalemu ndipo Baibulo limasonyeza kuti iye anakwaniritsa ulosi wa mulemba lalerowu. (Sal. 69:9) Koma sitinganene kuti Nyumba ya Ufumu ndi ‘nyumba ya Yehova’ ngati mmene zinalili ndi kachisi ku Yerusalemu. (2 Mbiri 5:13; 33:4) Ngakhale zili choncho, m’Baibulo muli mfundo zosonyeza zimene tiyenera kuchita polemekeza Nyumba ya Ufumu. w15 7/15 4:1, 2

Lachisanu, December 15

Valani chikondi.​—Akol. 3:14.

Kodi mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu tidzakwanitsa kuchita zinthu mwachikondi? Tiyenera kuyesetsa panopa kukhala ndi mtima wokhululuka kuti tisadzavutike pa nthawiyo. (Akol. 3:12, 13) N’kutheka kuti m’dziko latsopano sitizidzapeza chilichonse pa nthawi imene tikufuna. Tidzafunika kukhalabe ndi mtima woyamikira ndiponso wokhutira ndi zilizonse zimene tapatsidwa. Choncho makhalidwe amene Yehova akutiuza kuti tikhale nawo panopa adzafunikanso m’dziko latsopano. Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwinowa ndiye kuti tikukonzekera zimene tidzachite kwamuyaya. Tikamatero timasonyeza kuti tikuyembekezera ndiponso kukonzekera ‘dziko latsopano limene likubweralo.’ (Aheb. 2:5; 11:1) Timasonyezanso kuti tikufunitsitsa kudzakhala m’dziko lachilungamo limene aliyense azidzamvera Yehova. w15 8/15 3:11, 12

Loweruka, December 16

Yendanibe mogwirizana [ndi Yesu].​—Akol. 2:6.

Zipatso zingakhale zosiyanasiyana koma pali zinthu zina zofanana zimene zimaonetsa kuti zipatsozo ndi zakupsa. Nawonso Akhristu olimba akhoza kukhala osiyana mitundu, mayiko, msinkhu kapena zimene achita pa moyo wawo. Akhozanso kusiyana chikhalidwe kapena zimene amakonda. Koma pali makhalidwe ena amene onsewa amakhala nawo omwe amasonyeza kuti ndi Akhristu olimba. Kodi ena mwa makhalidwe amenewo ndi ati? Mkhristu wolimba amayesetsa ‘kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri.’ (1 Pet. 2:21) Yesu ananena kuti tiyenera kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse ndi maganizo athu onse. Ananenanso kuti tiyenera kukonda anzathu mmene timadzikondera tokha. (Mat. 22:37-39) Mkhristu wolimba amayesetsa kutsatira malangizo amenewa. Iye amasonyeza kuti kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso kukonda kwambiri anzake, ndi kofunika kwambiri. w15 9/15 1:3-5

Lamlungu, December 17

Pamaso pa Mulungu, takhala chitsanzo chabwino kwa chikumbumtima cha munthu aliyense.​—2 Akor. 4:2.

Chikumbumtima chikhoza kutilimbikitsanso kuchita ntchito zabwino osati kungopewa zoipa. Ntchito yabwino komanso yofunika kwambiri ndi yolalikira. Chikumbumtima cha Paulo chinkamulimbikitsa kugwira ntchito imeneyi. Iye anati: “Ndinalamulidwa kutero. Ndithudi, tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!” (1 Akor. 9:16) Ifenso tikamatsanzira Paulo chikumbumtima chathu chimatiuza kuti tikuchita bwino. Tikamalalikira timathandizanso anthu ena kuti chikumbumtima chawo chiziwatsogolera bwino. Chikumbumtima chathu chikhoza kutithandiza kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo za Yehova. Koma chofunika ndi kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, kusinkhasinkha zimene taphunzirazo komanso kuzitsatira. Tikatero tidzaphunzitsa chikumbumtima chathu ndipo chidzayamba kutitsogolera bwino pa moyo wathu. w15 9/15 2:16, 18

Lolemba, December 18

Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda.​—Miy. 3:12.

Yosefe, Mose ndiponso Davide anakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Koma Yehova sanawasiye ndipo zimene anaphunzira pa nthawi ya mavutowo, zinawathandiza kuti iye adzawagwiritse ntchito pa maudindo aakulu. Tikamawerenga nkhani ngati zimenezi timaoneratu kuti Yehova amatikonda kwambiri. Yehova amatisonyezanso chikondi tikalakwitsa. Iye amatilangiza ndipo tikamvera malangizo akewo n’kulapa, ‘amatikhululukira ndi mtima wonse.’ (Yes. 55:7) Zimene Davide ananena zimasonyeza kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri. Iye anati: ‘Akukukhululukira zolakwa zako zonse ndipo akukuchiritsa matenda ako onse. Akuwombola moyo wako kudzenje, akukuveka kukoma mtima kosatha ndi chifundo ngati chisoti chachifumu.’ (Sal. 103:3, 4) Choncho tiyenera kumvera malangizo a Yehova podziwa kuti iye amatilangiza chifukwa chotikonda.​—Sal. 30:5. w15 9/15 4:13, 14

Lachiwiri, December 19

Mariya . . . ankamvetsera mawu [a Yesu].​—Luka 10:39.

Marita anatanganidwa ndi kukonzera Yesu chakudya. Ndiyeno ataona kuti Mariya sakumuthandiza anayamba kudandaula. Yesu anaona kuti Marita akukonza chakudya chambiri ndipo anamuuza mokoma mtima kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri.” Kenako anamuuza kuti akhoza kungokonza chakudya chochepa. Atatero, anayamikira Mariya ponena kuti: “Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.” (Luka 10:38-42) N’kutheka kuti Mariya akanaiwala mwamsanga zimene anadya tsikulo koma sakanaiwala mpaka kalekale zimene Yesu ananena pomuyamikira komanso zimene anamuphunzitsa. Zikuonekanso kuti Marita anamvera malangizo a Yesu ndipo ankayesetsa kutumikira Yehova mokhulupirika pa moyo wake wonse. Tikutero chifukwa chakuti patapita zaka zoposa 60, mtumwi Yohane ananena kuti: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake.”​—Yoh. 11:5. w15 10/15 3:3, 4

Lachitatu, December 20

Mphamvu yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu.​—2 Akor. 4:7.

Pali umboni wotsimikizira kuti Yehova akuthandiza anthu masiku ano. Anthu ambiri amene amapemphera kuti Mulungu awathandize amaona kuti akuwathandizadi. (Sal. 53:2) Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Allan ankalalikira pachilumba chinachake ku Philippines. Ndiyeno atakumana ndi mayi wina, anangodabwa kuti mayiyo wayamba kulira. Allan anati: “Patsikuli m’mawa mayiyu anapempha Yehova kuti amuthandize kukumana ndi a Mboni. Choncho ataona kuti Mulungu anayankha pemphero lake mwamsanga, zinamukhudza kwambiri moti analira.” Pasanathe chaka, anadzipereka kwa Yehova. Akhristu ambiri anaona Mulungu akuwathandiza pamene ankayesetsa kusiya makhalidwe oipa monga kusuta, kumwa mankhwala osokoneza ubongo kapena kuonera zolaula. Ena a iwo anayesetsa mobwerezabwereza kuti asiye zinthu zoipazo paokha koma analephera. Ndiyeno atapempha Yehova kuti awathandize, iye anawapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” yomwe inawathandiza kusiya makhalidwewo.​—Sal. 37:23, 24. w15 10/15 1:10, 11

Lachinayi, December 21

Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.​—Aef. 5:16.

Anthu ena amadzuka m’mawa kwambiri kuti awerenge Baibulo, kuganizira zimene awerengazo ndiponso kupemphera. Ena amachita zimenezi masana pa nthawi yopuma, apo ayi madzulo kapena usiku asanakagone. Palinso anthu ena amene amawerenga Baibulo m’mawa ndi madzulo omwe. Choncho tinganene kuti iwo ‘amaliwerenga usana ndi usiku.’ (Yos. 1:8) Koma mfundo yofunika ndi yakuti tsiku lililonse tiziyesetsa kupeza mpata wowerenga Mawu a Mulungu n’kumawaganizira. Baibulo limalonjeza kuti Yehova adzadalitsa anthu amene amaganizira Mawu ake ndiponso kuwatsatira. (Sal. 1:1-3) Paja Yesu ananena kuti: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.” (Luka 11:28) Chofunika kwambiri n’chakuti tikamaganizira Mawu a Mulungu tsiku lililonse tidzatha kulemekeza Yehova. Ndiyeno iye adzatithandiza kukhala osangalala panopa komanso adzatipatsa moyo wosatha m’dziko latsopano.​—Yak. 1:25; Chiv. 1:3. w15 10/15 4:17, 18

Lachisanu, December 22

Petulo anamutengera pambali ndi kuyamba kum’dzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.”​—Mat. 16:22.

Mtumwi Petulo anauza Yesu kuti adzikomere mtima n’cholinga choti asaphedwe. Koma Yesu anadziwa kuti maganizowa ndi olakwika. Choncho anathandiza Petulo komanso ophunzira ena onse kudziwa ubwino wa kudzipereka ndiponso kuipa kwa mtima woopa kuchita zimene Mulungu akufuna. (Mat. 16:21-27) Petulo anamvetsa mfundoyi ndipo anaphunzirapo kanthu. (1 Pet. 2:20, 21) Inunso muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wozindikira n’cholinga choti muzidziwa mmene mungathandizire ana anu. (Sal. 32:8) Mwachitsanzo, n’chiyani chingasonyeze kuti chikhulupiriro cha mwana wanu chayamba kuchepa? Kodi wayamba kumangodandaula za abale ndi alongo? Kapena kodi akuoneka kuti akukubisirani zinazake? N’zoona kuti si bwino kufulumira kuganiza kuti akuchita machimo ena akuluakulu ndipo wayamba moyo wachiphamaso. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti muzinyalanyaza ngati akuonetsa zizindikiro zoti ali ndi vuto linalake. w15 11/15 2:12, 13

Loweruka, December 23

Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kuleza mtima. . . . Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.​—Akol. 3:12, 14.

Kukondana ndiponso kugwirizana kwa anthu a Yehova kumasonyeza kuti chipembedzo chawo ndi choona. Paja Yesu anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Mtumwi Yohane analembanso kuti: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake. Pakuti uwu ndi uthenga umene munamva kuyambira pa chiyambi, kuti tizikondana.” (1 Yoh. 3:10, 11) A Mboni za Yehova amakondana komanso kugwirizana ndipo izi zimasonyeza kuti iwo ndi Akhristu enieni. Zimasonyezanso kuti Mulungu akuwagwiritsa ntchito kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi.​—Mat. 24:14. w15 11/15 4:10, 11

Lamlungu, December 24

Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.​—Miy. 25:11.

N’zoona kuti zikhalidwe komanso zikhulupiriro za anthu zimasiyanasiyana. Komabe chofunika ndi kudziwa nthawi yoyenera kulankhula. Nthawi zina munthu akhoza kunena zinthu zotikhumudwitsa ngakhale kuti sichinali cholinga chake. Zikatere ndi bwino kuganiza kaye ngati tiyenera kumuyankha kapena ayi. Ngati taona kuti tifunika kumuyankha, tiyenera kudikira kuti mtima wathu ukhale kaye pansi. (Miy. 15:28) Tizidziwanso nthawi yabwino youza achibale athu omwe si Mboni uthenga wa m’Baibulo. Ngakhale kuti timafuna kuti achibale athuwa adziwe Yehova, tiyenera kukhala oleza mtima komanso osamala. Tikamayesetsa kulankhula mawu abwino pa nthawi yoyenera, achibale athu angayambe kumvetsera uthenga wathu. w15 12/15 3:6, 8, 9

Lolemba, December 25

Zimenezi zatiphunzitsa . . . kukhala amaganizo abwino, . . . m’nthawi ino.​—Tito 2:12.

Tiyenera kuganiza bwino makamaka ngati taona kuti malangizo ena okhudza mankhwala enaake ndi okayikitsa. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi amene akufuna kundipatsa mankhwalawa angafotokoze bwinobwino mmene amagwirira ntchito? Kodi zimene akufotokozazi ndi zomveka? Nanga madokotala amaona kuti mankhwalawa ndi othandizadi?’ (Miy. 22:29) Mwachitsanzo, munthu angatiuze kuti anthu a m’mayiko ena angotulukira kumene mankhwalawo ndipo madokotala ambiri sanawadziwe. Kodi zimenezi tiyenera kuzikhulupirira? Nthawi zinanso anthu ena sangafotokoze bwinobwino kumene mankhwala awo amachokera kapena amati pali mphamvu inayake imene imachititsa kuti mankhwalawo azigwira ntchito. Tiyenera kusamala kwambiri ndi zoterezi chifukwa Mawu a Mulungu amaletsa kugwiritsa ntchito “mphamvu zamatsenga.”​—Yes. 1:13; Deut. 18:10-12. w15 12/15 4:16

Lachiwiri, December 26

Mwa onse obadwa kwa akazi, sanabadwepo wamkulu woposa Yohane M’batizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.​—Mat. 11:11.

M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri okhulupirika amene mzimu woyera unkawathandiza, koma sanapite kumwamba. Mmodzi wa anthu amenewa ndi Yohane M’batizi. Yesu anamuyamikira kwambiri komabe ananena kuti sali m’gulu la anthu opita kumwamba. Nayenso Davide ankathandizidwa kwambiri ndi mzimu woyera. (1 Sam. 16:13) Iye anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo analemba nawo Baibulo. (Maliko 12:36) Komabe mtumwi Petulo ananena kuti: “Davide sanakwere kumwamba.” (Mac. 2:34) Ngakhale kuti mzimu woyera unathandiza anthuwa kuchita zinthu zambiri, sunawachititse kuona kuti asankhidwa kuti adzapita kumwamba. Komabe izi sizikutanthauza kuti anthuwa anali ndi vuto linalake. Yehova adzawaukitsa kuti adzakhale m’Paradaiso padziko lapansi.​—Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15. w16.01 3:16

Lachitatu, December 27

Ine ndi Atate ndife amodzi.​—Yoh. 10:30.

Tikamagwira ntchito ndi anthu amene timawakonda, timayamba kuwadziwa bwino ndiponso kugwirizana nawo kwambiri. Timadziwanso zolinga zawo pa moyo komanso zimene akufuna kuchita kuti akwaniritse zolingazo. Yesu anagwira ntchito ndi Yehova kwa zaka mabiliyoni ambiri ndipo anayamba kukondana naye kwambiri. Iye ndi Atate wake ankagwirizana kwambiri ndipo ankasangalala kugwira ntchito limodzi. Yesu anapempha Yehova kuti aziyang’anira ophunzira ake. Pofotokoza chifukwa chake, anati: “Kuti akhale amodzi mmene ife tilili.” (Yoh. 17:11) Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo komanso kugwira ntchito yolalikira, timayamba kuzindikira makhalidwe abwino a Mulungu. Timaonanso kuti zinthu zimatiyendera bwino tikamamukhulupirira komanso kutsatira malangizo ake. Tikamayesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, nayenso amatiyandikira. (Yak. 4:8) Timayambanso kukondana kwambiri ndi abale ndi alongo athu. Zili choncho chifukwa timakhala ndi zolinga zofanana, timalalikira nawo limodzi, kusangalala nawo limodzi komanso timalimbikitsana tikakumana ndi mavuto. w16.01 5:9, 10

Lachinayi, December 28

Bwerera naye limodzi.​—Rute 1:15.

Rute anali wa ku Mowabu ndipo ankafunika kusankha kubwerera ku Mowabuko kapena kupita ku Betelehemu limodzi ndi apongozi ake. (Rute 1:1-8, 14) Makolo komanso achibale ake ankakhala ku Mowabu. Choncho iye akanaona kuti ndi bwino kubwerera kwawoko kuti achibale ake azikamusamalira. Komanso ankadziwa bwino anthu a ku Mowabu ndiponso chikhalidwe ndi chilankhulo chawo. Koma akanapita ku Betelehemu zonse zikanakhala zachilendo. Naomi ankaonanso kuti Rute akapita ku Betelehemu sakapeza mwamuna. Choncho anauza Rute kuti abwerere ku Mowabu. Ndiye kodi Rute anatani? Iye anasankha mosiyana ndi Olipa. Paja Olipa anabwerera “kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.” (Rute 1:9-15) Koma Rute sanafune kubwerera kwawo kuti akayambirenso kulambira milungu yonyenga. w16.02 2:4, 5

Lachisanu, December 29

Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.​—Mika 6:8.

Sauli ndi asilikali ake 3,000 anali m’chipululu cha Yudeya ndipo ankasakasaka Davide kuti amuphe. Tsiku lina usiku, Davide ndi anthu ake anafika pamalo amene Mfumu Sauli ndi asilikali ake ankagona. Anapeza onse ali m’tulo ndipo Davide ndi Abisai anayenda monyang’ama mpaka kukafika pamene Sauli anagona. Kenako Abisai anauza Davide kuti: “Ndilole chonde, ndimubaye ndi kumukhomerera pansi ndi mkondo kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.” Koma zimene Davide anayankha zinali zodabwitsa. Iye anati: “Ayi, usamuphe. Kodi ndani anatambasula dzanja lake ndi kupha wodzozedwa wa Yehova, n’kukhala wopanda mlandu? . . . Kwa ine, n’zosatheka! Sindingachite zimenezi pamaso pa Yehova. Sindingatambasule dzanja langa ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.” (1 Sam. 26:8-12) Davide ankadziwa zimene ankayenera kuchita kuti akhale wokhulupirika kwa Yehova. Ankaona kuti ayenera kulemekeza Sauli ndipo sayenera kumupha. Zili choncho chifukwa Sauli anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Masiku anonso Mulungu amafuna kuti atumiki ake azikhala ‘okhulupirika’ kwa iye komanso azilemekeza anthu audindo. w16.02 4:1, 2

Loweruka, December 30

Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.​—Sal. 40:8.

Kodi ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira zobatizidwa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti kubatizidwa ndi mwayi waukulu kwambiri. Komabe kubatizidwa ndi nkhani yaikulu imene muyenera kuiganizira bwino. Munthu amabatizidwa posonyeza kuti wadzipereka kwa Yehova. Amamulonjeza kuti adzamutumikira moyo wake wonse komanso azichita zofuna za Yehovayo osati zake. Choncho munthu asanabatizidwe ayenera kutsimikizira kuti wakonzekadi kudzipereka kwa Yehova, akufunadi kuchita zimenezi komanso akumvetsa tanthauzo la kudzipereka kwa Yehova. Ndiye kodi mungatani ngati mukuona kuti si inu wokonzeka kubatizidwa? Nanga mungatani ngati inuyo mukufuna kubatizidwa koma makolo anu akuona kuti muyenera kuyembekeza kuti muphunzire kaye zinthu zina? Simuyenera kukhumudwa, koma yesetsani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova kuti mubatizidwe pasanapite nthawi yaitali. w16.03 2:1, 2

Lamlungu, December 31

Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira.​—2 Akor. 6:14.

Pali Akhristu ena omwe anakhala a Mboni atakwatirana kale ndi munthu wosatumikira Yehova ndipo mnzawoyo sanakhalebe wa Mboni. Anthu amenewa ayenera kuyesetsa kuti banja lawo likhale lolimba. Kuti izi zitheke ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo nthawi zonse. Koma kuchita zimenezi sikophweka. Masiku ano Satana akulimbana kwambiri ndi mabanja. Choncho atumiki a Mulungu ayenera kuyesetsa kuti akhale ndi banja logwirizana. Kaya mwakhala m’banja zaka zingati, muziganizira zimene mungachite kapena kulankhula kuti mulimbitse banja lanu. Komanso achikulire amene akhala m’banja zaka zambiri angathandize mabanja a achinyamata. Angathe kuwaitana kuti adzakhale nawo pa kulambira kwawo kwa pabanja. Ndiyeno iwo akaona mmene achikulirewo amachitira zinthu, angazindikire kuti kaya anthu akhala m’banja kwa zaka zambiri bwanji, ayenera kusonyezana chikondi komanso kuchita zinthu mogwirizana.​—Tito 2:3-7. w16.03 3:14, 15

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena