February
Lachinayi, February 1
Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake.—Yak. 1:4.
Kodi kupirira kumamaliza kugwira “ntchito” iti? Kumatithandiza kukhala “okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.” (Yak. 1:4) Mayesero amatithandiza kudziwa zimene sitichita bwino. Koma tikawapirira tingati timakhala okwanira mbali zonse. Mwachitsanzo, tikakumana ndi mayesero n’kupirira, timaphunzira kukhala oleza mtima, oyamikira komanso achifundo. Kupirira kumatithandiza kuti tikhale Akhristu okhulupirika. Choncho tikakumana ndi mayesero tisamagonje n’kusiya kutsatira mfundo za m’Baibulo n’cholinga choti mavutowo athe. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mukuyesetsa kuti musamaganizire zinthu zoipa? Simuyenera kugonja. M’malomwake muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni. Zikatere mumaphunzira kukhala odziletsa kwambiri. Nanga mungatani ngati mukutsutsidwa ndi wachibale amene si wa Mboni? Musagonje ndipo pitirizani kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Musaiwale kuti tikamapirira mayesero, Yehova amatidalitsa.—Aroma 5:3-5; Yak. 1:12. w16.04 2:15, 16
Lachisanu, February 2
Modzichepetsa, [muziona] ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.
Anthu ambiri amakonda kwawo kumene amachokera komanso mtundu ndi chikhalidwe chawo. Koma kupanda kusamala, zimenezi zingachititse kuti tisamaone anthu komanso maboma mmene Mulungu amawaonera. N’zoona kuti Mulungu safuna kuti tizichita manyazi ndi chikhalidwe chathu. Ndipotu zimakhala zosangalatsa anthu azikhalidwe zosiyanasiyana akakhala pamodzi. Koma tiyenera kukumbukira kuti Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana. (Aroma 10:12) Choncho tisamanyadire kwambiri dziko kapena mtundu wathu mpaka kuyamba kuganiza kuti ndife apamwamba. Maganizowa angatichititse kuti tigonje mosavuta pakabuka nkhani zokhudza ndale. Zoterezi zinachitikanso m’nthawi ya atumwi. (Mac. 6:1) Ndiye kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kamtima konyada? Tiyerekeze kuti m’bale wochokera kudziko lina wakupatsani malangizo. Kodi mungakane malangizowo n’kumaganiza kuti, ‘Munthu wobwera sangatiuze zochita’? M’malomwake tiyenera kutsatira malangizo a m’Malemba amene ali mulemba la lero. w16.04 4:12, 13
Loweruka, February 3
Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.—Luka 4:43.
Yesu ankalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” ndipo amafuna kuti otsatira ake azichitanso chimodzimodzi. Ndiyeno kodi ndi gulu liti limene likulalikira uthengawu kwa “anthu a mitundu yonse”? (Mat. 28:19) Ndi a Mboni za Yehova okha basi. Wansembe wina yemwe wakhala akuchita umishonale m’mayiko ambiri anauza m’bale wina kuti ankafunsa a Mboni za Yehova m’dziko lililonse limene anapita kuti amuuze uthenga umene amalalikira. Wansembeyo anati: “Onse ndi opusa chifukwa ankandiyankha mofanana kuti: ‘Timalalikira uthenga wabwino wa Ufumu.’” Komatu zimenezi sizikusonyeza kuti a Mboni ndi opusa. Zikungosonyeza kuti amalankhula mogwirizana. (1 Akor. 1:10) M’pake kuti magazini yathu ya Nsanja ya Olonda imalengezanso Ufumu wa Yehova womwewu. Magaziniyi ikupezeka m’zilankhulo 254 ndipo magazini 59 miliyoni amasindikizidwa mwezi uliwonse. Palibenso magazini ena amene amasindikizidwa ochuluka chonchi. w16.05 2:6
Lamlungu, February 4
Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake.—2 Akor. 9:7.
Tiyerekeze kuti wofalitsa akufuna kuyamba upainiya wokhazikika. Ndiyeno kuti akwanitse angayambe kukhala moyo wosalira zambiri. Pa nthawi imodzimodziyo angamakayikire ngati angasangalaledi akakhala ndi zinthu zochepa. N’zoona kuti m’Baibulo mulibe lamulo loti tizichita upainiya ndipo n’zotheka kungokhala wofalitsa wokhulupirika. Koma Yesu ananena kuti anthu amene amalolera kusiya zinthu zina chifukwa cha Ufumu adzadalitsidwa. (Luka 18:29, 30) Malemba amanenanso kuti Yehova amasangalala kwambiri tikamapereka “nsembe zaufulu” ndiponso tikamamutumikira mokondwera. (Sal. 119:108) Ndiyeno wofalitsa ataganizira mfundo za m’malembawa komanso kupemphera kuti Mulungu amutsogolere akhoza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyi. Izi zingathandize kuti asankhe zinthu zimene angakwanitse ndipo Yehova angamudalitse kwambiri. w16.05 3:13
Lolemba, February 5
Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako, asanafike masiku oipa.—Mlal. 12:1.
Mavuto ena amene amafotokozedwa m’nkhani za achinyamata amachitikiranso munthu aliyense. Tonsefe timafunika kufotokoza zimene timakhulupirira, kudziletsa, kusatengera zochita za anzathu komanso kusankha bwino zosangalatsa ndi anthu ocheza nawo. Zinthu zonsezi zimafotokozedwa bwino m’nkhani zimene amalembera achinyamata. Ndiye kodi achikulire ayenera kuganiza kuti akawerenga nkhani za achinyamata anyozeka? Ayi. N’zoona kuti nkhanizi zimalembedwa m’njira yoti ziwafike pa mtima achinyamata. Koma malangizo ake amachokera m’Baibulo ndipo akhoza kuthandiza munthu aliyense. Nkhani zimene amalembera achinyamata zimawathandizanso kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.—Mlal. 12:13. w16.05 5:15, 16
Lachiwiri, February 6
Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.—Deut. 6:4, 5.
Mfundo yoti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi” ndi yofunika kwambiri. Inathandiza Aisiraeli kupirira mavuto osiyanasiyana polowa m’Dziko Lolonjezedwa. Ifenso tikamakumbukira mfundoyi, tidzatha kupirira mavuto amene tingakumane nawo pa chisautso chachikulu n’kulowa m’Paradaiso. Choncho tiyeni tipitirize kulambira Yehova yekha. Tizimukonda ndiponso kumutumikira ndi mtima wonse komanso tiziyesetsa kukhalabe ogwirizana. Tikamachita zimenezi tidzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu, onena za anthu omwe adzaweruzidwe kuti ndi nkhosa akuti: “Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”—Mat. 25:34. w16.06 3:2, 20
Lachitatu, February 7
Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse.—Yer. 17:9.
Mtima wonyada ungachititse kuti tizidziona kuti ndife olungama n’kukhala ngati dongo louma. Kodi inuyo munakhumudwapo chifukwa cha zochita za Mkhristu wina kapena chifukwa choti mwasiyitsidwa udindo winawake? Ngati ndi choncho kodi munatani? Kodi kamtima kodzikuza kanayamba kuonekera? Kapena munkafunitsitsa kukhalanso pa mtendere ndi anzanuwo komanso kukhala okhulupirika kwa Yehova? (Sal. 119:165; Akol. 3:13) Chizolowezi chochita machimo mwamseri, chingachititse kuti tizilephera kutsatira malangizo a Mulungu. Kenako tingamaone kuti palibe vuto lililonse tikachita tchimo. (Mlal. 8:11) M’bale wina amene anali ndi chizolowezi choonera zolaula anati: “Ndinayamba mtima wotsutsa zimene akulu ankachita.” Chizolowezi chakechi chinkawononga kwambiri mtima wake. Kenako zinadziwika kuti ankaonera zolaula ndipo anathandizidwa. N’zoona kuti tonsefe si angwiro. Koma tikakhala ndi chizolowezi chomangotsutsa ena kapena chodzikhululukira tikachita tchimo, mtima wathu ukhoza kuipa kwambiri. w16.06 2:5, 6
Lachinayi, February 8
Lekani kudera nkhawa moyo wanu.—Mat. 6:25.
Anthu amene Yesu ankawaphunzitsa ankadera nkhawa zinthu zosafunika kuzidera nkhawa. Ndiyeno anawauza kuti asiye ndipo anapereka chifukwa chomveka. Munthu akamadera nkhawa kwambiri zinthu zina, akhoza kusokonezeka n’kuyamba kuiwala zinthu zokhudza ubwenzi wake ndi Yehova. Yesu ankaona kuti nkhaniyi ndi yaikulu ndipo anachenjeza ophunzira ake za msampha umenewu maulendo 4 pa ulaliki wake wapaphiri. (Mat. 6:27, 28, 31, 34) Yesu ankadziwa zinthu zimene anthu amafunikira tsiku lililonse. Komanso ankadziwa mavuto amene anthu adzakumane nawo m’masiku otsiriza ano, omwe Baibulo limati ndi “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Ena mwa mavutowa ndi monga njala, umphawi, kusowa kwa ntchito komanso kukwera mitengo kwa zinthu. Koma Yesu ankadziwa kuti ‘moyo ndi wofunika kuposa chakudya ndipo thupi ndi lofunika kuposa chovala.’ w16.07 1:8, 9
Lachisanu, February 9
Ndinakhala mtumiki wa zimenezi mogwirizana ndi mphatso yaulere ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.—Aef. 3:7.
Anthufe tikanakhala kuti timatha kuchita bwinobwino zonse zimene Mulungu amafuna, bwenzi kuli koyeneradi kuti azitisonyeza kukoma mtima kwakukulu. Koma nthawi zina timalakwitsa. Mfumu Solomo analemba kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlal. 7:20) Nayenso mtumwi Paulo anati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” Ananenanso kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” (Aroma 3:23; 6:23a) Choncho tonsefe timayenera kufa basi. Koma Yehova amatikonda ndipo anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu. Anatumiza “Mwana wake wobadwa yekha” kuti adzatifere ndipo iyi ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. (Yoh. 3:16) Paulo analemba kuti Yesu anavekedwa “ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anazunzika mpaka imfa. Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Aheb. 2:9) Choncho “mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23b. w16.07 3:3, 4
Loweruka, February 10
Ndimupangira womuthandiza.—Gen. 2:18.
Ukwati ndi nkhani yaikulu kwambiri. Choncho tiyeni tikambirane mmene unayambira komanso cholinga chake. Izi zitithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhaniyi komanso kuti tizisangalala m’banja. Yehova atalenga Adamu, anamubweretsera nyama zonse kuti azitchule mayina. Koma Adamuyo “analibe womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” Ndiyeno Mulungu anamugonetsa tulo tofa nato n’kumuchotsa nthiti. Kenako anamupangira mkazi pogwiritsa ntchito nthitiyo n’kumubweretsera. (Gen. 2:20-24) Choncho Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati. Yesu anasonyeza kuti Yehova ndi amene ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” (Mat. 19:4, 5) Zimene Yehova anachita pogwiritsa ntchito nthiti ya mwamuna n’kupanga mkazi, zinasonyeza kuti ankafuna kuti anthuwo azikondana komanso kugwirizana. Sanafune kuti iwo adzalekane kapena kuchita mitala. w16.08 1:1, 2
Lamlungu, February 11
[Yesu] anachoka kumeneko n’kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira kumizinda ina.—Mat. 11:1.
Yesu ankakonda kukambirana ndi anthu za Ufumu. Mwachitsanzo, atafika pachitsime cha Yakobo, pafupi ndi mzinda wa Sukari, anakambirana ndi mayi wina mfundo zambiri. (Yoh. 4:5-30) Iye anakambirananso ndi Mateyu Levi yemwe anali wokhometsa misonkho. Mateyuyo anavomera kukhala wophunzira wa Yesu. Ndiyeno atafika kunyumba kwawo, Mateyu ndi anzake anamvetsera kwa nthawi ndithu pamene Yesu ankawaphunzitsa. (Mat. 9:9; Luka 5:27-39) Pa nthawi ina, Natanayeli ankakayikira anthu onse ochokera ku Nazareti. Komabe Yesu anacheza naye bwinobwino ndipo izi zinamuthandiza kuti asinthe maganizo. Iye anafuna kumva zambiri zimene Yesu ankaphunzitsa ngakhale kuti Yesuyo ankachokera ku Nazareti. (Yoh. 1:46-51) Nafenso tiyenera kuthandiza atsopano kuti aziyesetsa kukambirana ndi anthu mwaubwenzi. Akamatero adzasangalala kuona kuti anthu akumvetsera uthenga wawo. w16.08 4:7-9
Lolemba, February 12
Mkazi asasiye mwamuna wake. . . . Mwamunanso asasiye mkazi wake.—1 Akor. 7:10, 11.
M’banja mukakhala mavuto aakulu kwa nthawi yaitali, ambiri amayamba kuganiza zopatukana kapena kuthetsa banjalo. Tisamaganize kuti kupatukana ndi nkhani yaing’ono. Tiyenera kudziwa kuti izi zimangowonjezera mavuto. Yesu atabwereza zimene Mulungu ananena zoti mwamuna amasiya makolo n’kukadziphatika kwa mkazi wake, anati: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:3-6; Gen. 2:24) Izi zikusonyeza kuti ngati mwamuna kapena mkazi akuganiza zothetsa banja ndiye kuti ‘akulekanitsa chimene Mulungu anamanga.’ Yehova amaona kuti okwatirana ayenera kukhala limodzi moyo wawo wonse. (1 Akor. 7:39) Kukumbukira kuti tonsefe tidzayankha kwa Mulungu, kungatithandize kuti tizithetsa mavuto zinthu zisanafike poipa. w16.08 2:10, 11
Lachiwiri, February 13
Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.—Aroma 12:21.
Adani athu akhoza kutiukira pa nthawi imene sitikuyembekezera kapena pamene tafooka kwambiri. Choncho tiyenera kukhala maso nthawi zonse. Mawu akuti “musalole kuti choipa chikugonjetseni” akusonyeza kuti tikhoza kugonjetsa zoipazo. Chongofunika ndi khama basi. Koma ngati sitili maso kapena tasiya kuchita khama, tikhoza kugonjetsedwa ndi Satana, dziko loipali komanso thupi lathu lochimwali. Tisalole kuti Satana atiopseze mpaka kufika posiya kumenya nkhondoyi. (1 Pet. 5:9) Kuti munthu apambane pa mpikisano ayenera kudziwa cholinga chake. Kuti ifenso tisangalatse Yehova n’kudalitsidwa, tiyenera kukumbukira nthawi zonse mawu a pa Aheberi 11:6 akuti: “Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “omufunafuna ndi mtima wonse” amasonyeza kuti pamafunika khama kwambiri.—Mac. 15:17. w16.09 2:4, 5
Lachitatu, February 14
Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.—1 Akor. 10:31.
M’Baibulo muli malangizo othandiza kuti tizisankha zovala zimene zingalemekeze Mulungu. Koma sikuti tonse timavala zofanana. Zili choncho chifukwa chakuti anthufe timasiyana zokonda komanso kapezedwe ka ndalama. Komabe tonse timafunika kuvala zovala zoyenera komanso zaukhondo. Zovalazo ziyeneranso kukhala zogwirizana ndi malo amene tili komanso chikhalidwe cha kuderalo. N’zoona kuti si zapafupi kusankha zovala zabwino moganizira mfundo zonse. Masiku ano, m’masitolo ambiri mumangopezeka zovala zamafashoni amakono ndipo munthu amafunika kuchita khama kuti apeze siketi, diresi, bulauzi, suti kapena thalauza yoyenera komanso yosathina. Koma tikamayesetsa kusankha zovala zoyenera, Akhristu anzathu amaona ndiponso amayamikira. Ifenso timasangalala podziwa kuti zovala zathu zikulemekeza Atate wathu wakumwamba ndipo sitidandaula ndi zimene ena angatinene. w16.09 3:15, 16
Lachinayi, February 15
Iye anatambasula kumpoto pamwamba pa malo opanda kanthu, ndipo anakoloweka dziko lapansi m’malere.—Yobu 26:7.
Ana amatha kuona zinthu m’maganizo mwawo. Choncho muzigwiritsa ntchito zitsanzo powaphunzitsa. Zitsanzo zabwino zingathandizenso ana kuti azikhulupirira kuti Baibulo ndi lolondola. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo yamulemba la leroli. Kodi mungatani kuti mwana wanu azikhulupirira zoti Yehova ndi amene anauzira Yobu kuti anene mawuwa? Si bwino kungomuuza mfundoyi koma muyenera kumuthandiza kuiganizira kwambiri. Mungamuuze kuti Yobu anakhala ndi moyo pa nthawi yomwe kunalibe zipangizo zoonera zakuthambo. Mwanayo azifotokoza mfundo zosonyeza kuti n’zosatheka kuti chinthu chachikulu ngati dziko chikhale m’malere. Mwina angagwiritse ntchito mpira kapena mwala posonyeza kuti chinthu cholemera chimafunika kukhala penapake osati m’malere. Kenako mungamuuze kuti nthawi ya Yobu anthu sankakhulupiriranso zoti dziko lili m’malere. Izi zingathandize mwanayo kuona kuti m’Baibulo munalembedwa zinthu zolondola pa nthawi yomwe anthu anali asanazitulukire.—Neh. 9:6. w16.09 5:9, 12
Lachisanu, February 16
Mumtima mwako ukukhulupirira.—Aroma 10:9.
Chikhulupiriro sichimangotanthauza kudziwa bwino madalitso amene Mulungu watilonjeza. Chimathandizanso kuti munthu azichita zinthu zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kukhulupirira kuti Mulungu ali ndi mphamvu zotipulumutsa kumatipangitsa kuti tiziuza ena uthenga wabwino. Kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro. Tiyeneranso kuonetsetsa kuti chikhulupiriro chathucho n’cholimba. Chikhulupiriro tingachiyerekezere ndi chomera. Kuti chomera chizikula bwino, timayenera kuchithirira nthawi zonse. Kupanda kutero chingafote kenako n’kufa. N’chimodzimodzinso ndi chikhulupiriro. Kupanda kuchisamalira chikhoza kufooka mpaka kutha. (Luka 22:32; Aheb. 3:12) Choncho nthawi zonse tiyenera kuonetsetsa kuti chikhulupiriro chathu ndi “cholimba” komanso “chikukula.”—2 Ates. 1:3; Tito 2:2. w16.10 4:4, 5
Loweruka, February 17
Mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu anapatsa anawa mayina ena. Danieli anamupatsa dzina lakuti Belitesazara.—Dan. 1:7.
Pamene Danieli ndi anzake anali ku ukapolo, Ababulo anawaphunzitsa “chinenero cha Akasidi” n’cholinga choti azitsatira chikhalidwe chawo. Komanso mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina achibabulo. (Dan. 1:3-7) Dzina limene anamupatsa Danieli linkanena za mulungu wa Ababulowo dzina lake Beli. Mwina Nebukadinezara ankafuna kuti Danieli aziganiza kuti Yehova anagonjetsedwa ndi mulungu wa Ababulo. (Dan. 4:8) Ngakhale kuti Danieli anapatsidwa mwayi woti azidya zakudya za mfumu, “anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa.” (Dan. 1:8) Iye anapitirizanso kuphunzira “mabuku” a chilankhulo chake. (Dan. 9:2) Izi zinamuthandiza kuti akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba. Choncho patatha zaka 70 kuchokera pamene anafika ku Babulo, ankadziwikabe ndi dzina lake lachiheberi.—Dan. 5:13. w16.10 2:7, 8
Lamlungu, February 18
Kulikonse kumene mzimu ukufuna kupita, zamoyozo zinali kupita kumeneko.—Ezek. 1:20.
Anthu ena amaganiza kuti akhoza kumvetsa Baibulo paokha. Koma Yesu wasankha “kapolo wokhulupirika” kuti azipereka chakudya chauzimu. (Mat. 24:45-47) Kuyambira mu 1919, Yesu wakhala akugwiritsa ntchito kapoloyu kuti athandize anthu ake kumvetsa Mawu a Mulungu komanso kuwatsatira. Tikamachita zimenezi timakhala oyera, amtendere komanso ogwirizana. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wokhulupirika kwa Yesu ndipo ndimatsatira malangizo a kapolo amene akumugwiritsa ntchito?’ Baibulo limatithandiza kudziwa bwino za mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. Mwachitsanzo, Ezekieli anaona m’masomphenya Yehova atakwera galeta ndipo galetali likuimira mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu (Ezek. 1:4-28) Panopa galeta la Yehovali likuthamanga kwambiri ndipo posachedwapa, Yesu limodzi ndi angelo adzawononga dziko loipali. Izi zidzathandiza kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe ndipo aliyense atsimikizire kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. w16.11 3:9, 10
Lolemba, February 19
Tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.—Aheb. 10:25.
Mofanana ndi Akhristu oyambirira, timasonkhana kuti tiphunzitsidwe komanso tilimbikitsidwe. (1 Akor. 14:31) Ngakhalenso anthu amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali amafunika kulimbikitsidwa. Taganizirani chitsanzo cha Yoswa. Iye anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. Koma Mulungu anauza Mose kuti amulimbikitse. Anati: “Uike Yoswa kukhala mtsogoleri ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, chifukwa ndiye adzawolotsa anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.” (Deut. 3:27, 28) Yoswa anali atatsala pang’ono kutenga udindo waukulu wotsogolera Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Pa ntchitoyi anakumana ndi mavuto angapo ndipo pa nthawi ina gulu lake la nkhondo linagonjetsedwa. (Yos. 7:1-9) Ndiyetu m’pake kuti ankafunika kulimbikitsidwa. Choncho tiyeni nafenso tizilimbikitsa akulu komanso oyang’anira madera chifukwa amagwira ntchito yaikulu yosamalira nkhosa za Mulungu.—1 Ates. 5:12, 13. w16.11 1:12, 13
Lachiwiri, February 20
Bwera, ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikulu lokhala pamadzi ambiri.—Chiv. 17:1.
Ophunzira Baibulo anazindikira kuti si zokwanira kungouza achibale awo ndi anzawo kuti iwo achoka m’chipembedzo chonyenga. Ankaona kuti anthu onse ayenera kudziwa kuti Babulo Wamkulu ali ngati hule. Choncho kuyambira mu December 1917 mpaka chakumayambiriro kwa 1918 Ophunzira Baibulowa anagawira kapepala ka mutu wakuti, “Kugwa kwa Babulo.” Anagawira timapepala tokwana 10 miliyoni ndipo timapepalati tinathandiza anthu kudziwa zoona zokhudza Matchalitchi Achikhristu. Atsogoleri achipembedzo anakwiya koopsa ndi zimenezi koma Ophunzira Baibulowo sanafooke. Iwo ankafunitsitsa “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:29) Zonsezi zikusonyeza kuti Ophunzira Baibulo sanalowe mu ukapolo wa Babulo Wamkulu pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse. Koma pa nthawiyi n’kuti akutulukamo ndipo ankathandizanso ena kuti achite chimodzimodzi. w16.11 5:2, 4
Lachitatu, February 21
Otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.—Aroma 8:5.
Ena angaganize kuti apa akusiyanitsa Akhristu ndi anthu amene si Akhristu. Komatu musaiwale kuti kalata ya Pauloyi inkapita kwa ‘amene anali ku Roma monga okondedwa a Mulungu, oitanidwa kukhala oyera.’ (Aroma 1:7) Choncho Paulo ankafotokoza kusiyana pakati pa Akhristu amene ankayenda motsatira thupi, ndi Akhristu amene ankayenda motsatira za mzimu. Iye analemba kuti: “Pamene tinali kukhala mogwirizana ndi thupi, zilakolako za uchimo zimene zinaonekera chifukwa cha Chilamulo zinali kugwira ntchito m’ziwalo zathu.” (Aroma 7:5) Choncho ponena kuti anthu amene “amaika maganizo awo pa zinthu za thupi,” Paulo ankanena za anthu amene amangotsatira zilakolako za uchimo n’kumachita chilichonse chimene akufuna. w16.12 2:5, 7
Lachinayi, February 22
Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake.—Sal. 32:1.
Nthawi zina timakhala ndi nkhawa chifukwa cha zimene tinalakwitsa m’mbuyomu Pa nthawi ina Mfumu Davide ankaona kuti ‘zolakwa zake zakwera kupitirira mutu wake.’ Iye anati: “Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.” (Sal. 38:3, 4, 8, 18) Ndiye kodi Davide anatani? Iye anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo komanso amukhululukire. (Sal. 32:2, 3, 5) Nthawi zina timada nkhawa chifukwa cha mmene zinthu zilili panopa. Mwachitsanzo, pamene Davide ankalemba Salimo 55 n’kuti akuda nkhawa kuti aphedwa. (Sal. 55:2-5) Komabe sanalole nkhawa zakezo kumulepheretsa kuti azikhulupirira Yehova. M’malomwake anapemphera za nkhaniyo mochokera pansi pa mtima. Koma ankadziwanso kuti ayenera kuchita zinthu zina zimene zingamuthandize kuchepetsa nkhawa zakezo. (2 Sam. 15:30-34) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Davide? M’malo moda nkhawa kwambiri ndi vuto lathu, tizipemphera, kupeza njira zochepetsera nkhawa ndipo kenako tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. w16.12 3:14, 15
Lachisanu, February 23
Ndachimwira Yehova.—2 Sam. 12:13.
Davide anavomereza pamene mneneri wa Yehova dzina lake Natani anabwera kudzamudzudzula. Komanso iye anapemphera kwa Yehova, anavomereza machimo ake ndipo analapa. Anasonyezanso kuti ankafunitsitsa kuti Mulungu ayambirenso kumukonda. (Sal. 51:1-17) Davide sanalole kuti machimo ake amulepheretse kutumikira Mulungu, koma anangophunzirapo kanthu. Komanso anayesetsa kuti asadzabwerezenso machimowo. Patatha zaka zambiri anamwalira ali wokhulupirika ndipo Yehova akumukumbukirabe. (Aheb. 11:32-34) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikachita tchimo lalikulu, tiyenera kuvomereza tchimolo, kulapa kuchokera mumtima ndiponso kupempha Yehova kuti atikhululukire. (1 Yoh. 1:9) Tizifotokozeranso akulu kuti atithandize kukhalanso pa ubwenzi ndi Yehova. (Yak. 5:14-16) Tikachita zimenezi, timasonyeza kuti tikukhulupirira zoti Yehova angatikhululukire. Komabe, tiyenera kuphunzirapo kanthu n’kuyambiranso kutumikira Yehova mokhulupirika.—Aheb. 12:12, 13. w17.01 1:13, 14
Loweruka, February 24
Mundiletse kuchita modzikuza, ine mtumiki wanu.—Sal. 19:13.
Munthu ‘wodzikuza’ amachita zinthu zomwe si udindo wake ndipo nthawi zambiri amachita zimenezi chifukwa cha kunyada kapena chifukwa cholephera kuleza mtima. Popeza ndife ochimwa, tonsefe pa nthawi ina tinachitapo zinthu modzikuza. Koma chitsanzo cha Mfumu Sauli chikusonyeza kuti tikalola zimenezi kukhala chizolowezi, tingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Lemba la Salimo 119:21 limati Yehova ‘amadzudzula odzikuza.’ N’chifukwa chiyani zili choncho? Kukhala ndi chizolowezi chochita zinthu modzikuza n’koopsa. Tikutero pa zifukwa zitatu. Choyamba tikamachita zinthu modzikuza timasonyeza kuti sitilemekeza Yehova yemwe ndi Wolamulira wathu. Chachiwiri, tikamachita zinthu zomwe si udindo wathu, anthu ena sangasangalale ndipo tingathe kuyambana nawo. (Miy. 13:10) Chachitatu, zikadziwika kuti tachita zinthu modzikuza, tingachite manyazi. (Luka 14:8, 9) Apatu zikusonyezeratu kuti kudzikuza si kwabwino. M’pake kuti Malemba amatilimbikitsa kuti tikhale odzichepetsa. w17.01 3:4, 5
Lamlungu, February 25
Iwo achita okha zinthu zowawonongetsa, si ana ake, chilemacho n’chawo.—Deut. 32:5.
Popeza sanalinso wangwiro, Adamu sakanatha kusonyeza bwinobwino makhalidwe a Mulungu. Iye anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndipo anapatsira ana ake uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Ana ake analibenso mwayi woti n’kukhala ndi moyo wosatha. Komanso Adamu ndi Hava sakanatha kubereka ana angwiro ndipo n’chimodzimodzinso ndi ana awo. Kungoyambira nthawi imene Satana anachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe, iye sanasiyebe kusokoneza anthu. (Yoh. 8:44) Mulungu sanasiye kukonda anthu. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava sanamumvere, iye amafuna kuti anthu akhalebe naye pa ubwenzi. Mulungu safuna kuti aliyense adzafe. (2 Pet. 3:9) Choncho nkhani ya mu Edeni itangochitika, iye anakonza zoti ana a Adamu adzathe kukhalanso naye pa ubwenzi. Koma anachita izi popanda kuphwanya mfundo zake zachilungamo.—Yoh. 3:16. w17.02 1:12-14
Lolemba, February 26
Anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.—Miy. 13:10.
Tizitsanzira Yehova n’kumaganizira kwambiri zimene ena amachita bwino. Zimenezi zingatithandize kuti tizikhutira ndi udindo wathu m’gulu la Yehova. Komanso m’malo mofuna kuti anthu azimvera ifeyo nthawi zonse, tizifunsa maganizo awo kapena kutsatira zimene ena anena. Abale athu akapatsidwa udindo tizisangalala nawo. Komanso tizitamanda Yehova poona kuti akudalitsa ‘gulu lonse la abale m’dzikoli.’ (1 Pet. 5:9) Tikamaona zinthu mmene Mulungu amazionera, timakhala anthu ozindikira. Chikumbumtima chathu chikhoza kumagwira bwino ntchito ngati timakonda kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kutsatira zimene tikuphunzirazo. (1 Tim. 1:5) Tikamachita zimenezi timaphunziranso kuika patsogolo zofuna za anzathu. Ndiyeno ifeyo tikachita mbali yathu, Yehova ‘adzamalizitsa kutiphunzitsa’ kuti tikhale ndi makhalidwe abwino monga kudzichepetsa.—1 Pet. 5:10. w17.01 4:17, 18
Lachiwiri, February 27
Akulu otsogolera bwino apatsidwe ulemu waukulu, makamaka amene amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.—1 Tim. 5:17.
Anthu enanso oyenera kuwalemekeza ndi Akhristu anzathu. Ndipo tiyenera kulemekeza makamaka akulu amene amatitsogolera. Timawalemekeza mosatengera mtundu wawo, maphunziro awo, chuma chawo kapenanso kuti ndi otchuka kapena ayi. Baibulo limanena kuti akulu ndi “mphatso za amuna,” ndipo amagwira ntchito yaikulu posamalira anthu a Mulungu. (Aef. 4:8) Taganizirani ntchito imene akulu, oyang’anira dera, abale a m’Komiti ya Nthambi komanso a m’Bungwe Lolamulira amagwira. Abale ndi alongo a m’nthawi ya atumwi ankalemekeza kwambiri anthu amene Mulungu anawasankha kuti aziwatsogolera. Ifenso masiku ano timachita chimodzimodzi. Sikuti timawalemekeza mpaka kufika pokhala ngati tikuwalambira ndipo tikakumana nawo sitimakhala ngati takumana ndi angelo. Komabe timalemekeza abalewa chifukwa cha ntchito imene amagwira komanso kudzichepetsa kwawo.—2 Akor. 1:24; Chiv. 19:10. w17.03 1:13
Lachitatu, February 28
N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.—Maliko 10:18.
Zimene Yesu ananenazi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Herode Agiripa Woyamba anachita. Iye anakhala mfumu ya Yudeya patadutsa zaka 8 kuchokera pamene Yesu ananena mawuwa. Pa tsiku la msonkhano, Herode anavala “zovala zake zachifumu” n’kuyamba kulankhula. Anthu atamva mawu ake anafuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu ayi!” Herode ayenera kuti anasangalala ndi mawu amenewa. Koma “nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha, chifukwa sanapereke ulemerero kwa Mulungu. Ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira.” (Mac. 12:21-23) Kunena zoona, munthu wanzeru zake sangaganize kuti Herode anali mfumu yosankhidwa ndi Yehova. Koma nthawi zonse Yesu ankasonyeza kuti anasankhidwa ndi Mulungu ndipo ankatamanda Yehova chifukwa chakuti ndi Wolamulira Wamkulu wa anthu ake. Ulamuliro wa Yesu si wa zaka zochepa ayi. Paja iye ataukitsidwa ananena kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kenako anati: “Dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mat. 28:18-20. w17.02 3:20, 21