March
Lachinayi, March 1
Anathamangitsa Yefita.—Ower. 11:2.
Abale ake a Yefita anamuthamangitsa chifukwa choti anali mwana wa mayi wina. Anati sankayenera kulandira cholowa ngati mwana woyamba kubadwa. (Ower. 11:1-3) Koma Yefita atapemphedwa kuti akathandize abale akewo, anapita mosanyinyirika. (Ower. 11:4-11) Iye ankaona kuti kumenya nkhondo poyeretsa dzina la Yehova n’kofunika kwambiri kusiyana ndi kulimbana ndi abale akewo. Ankafunitsitsa kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwa iyeyo komanso kwa anthu ena. (Aheb. 11:32, 33) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yefita anachita? Mwina pali Mkhristu wina amene anakulakwirani kapena kukukhumudwitsani. Ngati ndi choncho, musalole kuti nkhani imeneyo ikulepheretseni kusonkhana kapena kutumikira Yehova limodzi ndi mpingo. Potengera chitsanzo cha Yefita, tizitsatira mfundo za Yehova n’kumachitabe zabwino ngakhale titakumana ndi mavuto.—Aroma 12:20, 21; Akol. 3:13. w16.04 1:7, 9, 10
Lachisanu, March 2
Sitikubwerera m’mbuyo.—2 Akor. 4:1.
Tiyenera kupirira osati kwa kanthawi chabe, koma mpaka mapeto. Tiyerekeze kuti anthu akwera sitima ndipo ikumira. Kuti munthu apulumuke, ayenera kusambira mpaka kumtunda. Ngati munthu wasambira kwa nthawi yaitali koma n’kutopa atatsala pang’ono kufika pamtunda akhoza kufa mofanana ndi munthu amene anangosambira pang’ono n’kusiya. Mofanana ndi zimenezi, kuti tidzalowe m’dziko latsopano tiyenera kupirira mpaka mapeto. Tiyenera kukhala ndi maganizo amene mtumwi Paulo anali nawo. Kawiri konse iye anati: “Sitikubwerera m’mbuyo.” (2 Akor. 4:16) Tisamakayikire kuti Yehova atithandiza kupirira mpaka mapeto. Paja Paulo ananena pa Aroma 8:37-39 kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi kudzera mwa iye amene anatikonda. Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” w16.04 2:17, 18
Loweruka, March 3
Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa.—Yak. 1:5.
Tizipempha nzeru kwa Yehova kuti tizitha kuzindikira zinthu zimene zingatichititse kuti tikhale osakhulupirika pa nkhani zokhudza ndale. Kodi muli m’ndende chifukwa chofuna kukhalabe okhulupirika? Ngati ndi choncho, mungapemphe Yehova kuti akupatseni mphamvu kuti mulimbe mtima komanso muthe kupirira mavuto alionse amene mungakumane nawo (Mac. 4:27-31) Yehova angakuthandizeni pogwiritsa ntchito Mawu ake. Mungawerenge ndi kuganizira kwambiri mavesi amene angakuthandizeni kuti musalowerere ndale. Ndi bwinonso kuloweza mavesi oterewa chifukwa angadzakuthandizeni pa nthawi imene mulibe Baibulo. Mawu a Mulungu amatithandizanso kuti tizikhulupirira kwambiri madalitso amene Ufumu udzabweretse. Izi zingatithandize kuti tipirire tikamayesedwa. (Aroma 8:25) Mukhozanso kusankha malemba amene amanena za zinthu zimene inuyo mudzasangalale nazo kwambiri m’Paradaiso. Kenako muziganizira mmene mudzasangalalire malembawo akadzakwaniritsidwa. w16.04 4:14, 15
Lamlungu, March 4
Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.—Mat. 10:8.
Atsogoleri a matchalitchi salalikira za Ufumu wa Mulungu. Akati anene za Ufumuwo, ambiri amangoti umakhala mumtima mwa Mkhristu aliyense. (Luka 17:21) Iwo sathandiza anthu kuzindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu. Sanenanso zoti Ufumuwo ndi umene udzathetse mavuto ndi zoipa zonse padzikoli. (Chiv. 19:11-21) M’malomwake amalimbikitsa anthu kukumbukira Yesu pa Khirisimasi ndi pa Isitala. Sadziwa ngakhale pang’ono zimene Yesu adzachite akamadzalamulira padzikoli. Sadziwa cholinga cholalikirira uthenga. Cholinga sichiyenera kukhala chongofuna kupeza ndalama komanso kumanga nyumba zogometsa. Choncho sitiyenera kuchita malonda ndi Mawu a Mulungu. (2 Akor. 2:17) Anthu amene amalalikira uthenga wabwino sayenera kugwira ntchitoyi n’cholinga chofuna kupeza phindu.—Mac. 20:33-35. w16.05 2:7, 8
Lolemba, March 5
Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.—1 Akor. 10:24.
Tiyerekeze kuti chovala chinachake chakusangalatsani komabe mukudziwa kuti chingakhumudwitse anthu ena mumpingo. Mukudziwanso kuti m’Baibulo mulibe lamulo loletsa chovalacho. Kodi mungadziwe bwanji maganizo a Yehova pa nkhaniyi? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru, osati kudzikongoletsa ndi masitayilo omangira tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali. Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera.” (1 Tim. 2:9, 10) Mfundo zapalembali zikukhudzanso amuna. Atumiki a Yehovafe sitimangoganizira zimene tikufuna koma timaganiziranso mmene ena angaonere zovala zathu. Kudzichepetsa komanso kukonda Akhristu anzathu kungapangitse kuti tiziwaganizira n’kumapewa kuwakhumudwitsa.—1 Akor. 10:23; Afil. 3:17. w16.05 3:14
Lachiwiri, March 6
Yehova, inu ndinu Atate wathu. Ife ndife dongo ndipo inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.—Yes. 64:8.
Adamu atachimwa, mwayi wokhala mwana wa Mulungu unathera pomwepo. Komabe ana ena a Adamu akhala akumvera ulamuliro wa Mulungu ndipo ali ngati “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Anthu amenewa asonyeza kuti amafuna kuti Yehova akhale Atate awo komanso kuti aziwaumba. Iwo akana kuumbidwa ndi Satana komanso kukhala ana ake. (Yoh. 8:44) Zimenezi zikutikumbutsa mawu amene Yesaya ananena omwe ali mulemba la leroli. Masiku anonso, anthu amene amalambira Yehova motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi amayesetsa kukhala ndi maganizo amenewa. Amaona kuti ndi mwayi waukulu kuumbidwa ndi Yehova komanso kukhala ana ake. Kodi inuyo muli ngati dongo lofewa lokonzeka kuumbidwa n’kukhala chinthu chamtengo wapatali pamaso pa Yehova? Nanga mumaona kuti Akhristu anzanu ali ngati chinthu choti chikuumbidwabe ndi Yehova? w16.06 1:2, 3
Lachitatu, March 7
Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro.—2 Akor. 13:5.
Tangotsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano ndipo chikhulupiriro chathu chikuyesedwa kwambiri. Choncho ndi bwino kudzifufuza ngati tidakali ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo tingadzifunse kuti, ‘Kodi timakhulupirira mawu a Yesu a pa Mateyu 6:33? Kodi zimene ndimasankha pa moyo wanga zimasonyeza kuti ndimakhulupiriradi mawuwa? Kodi ndimasankha kujomba kumisonkhano kapena mu utumiki n’cholinga choti ndikokere? Kodi ndingatani ngati mavuto azachuma atawonjezeka? Kodi ndidzalola kuti dzikoli lindikanikizire m’chikombole chake n’kusiya gulu la Yehova?’ Taganiziraninso za abale ndi alongo amene zimawavuta kutsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani zokhudza ochotsedwa, zosangalatsa kapena anthu ocheza nawo. Mungadzifunsenso kuti: ‘Kodi ine ndimachita bwanji pa nkhanizi?’ Ngati taona kuti tili ndi vuto, tiyenera kuyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Nthawi zonse tizidzifufuza pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. w16.06 2:8, 9
Lachinayi, March 8
Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.—Yes. 60:22.
Gulu la Mboni za Yehova ndi gulu lapadera padziko lonse. N’zoona kuti anthu ake si angwiro ndipo amalakwitsa zinthu zina. Koma Mulungu amawatsogolera ndi mzimu wake kuti gulu lawo lizikula komanso zinthu ziziyenda bwino. Pamene masiku otsiriza ankayamba mu 1914, atumiki a Mulungu padzikoli anali ochepa kwambiri. Koma Yehova anadalitsa ntchito yawo yolalikira ndipo m’zaka zotsatira, anthu mamiliyoni anayamba kuphunzira Baibulo n’kukhala Mboni za Yehova. Yehova ananeneratu zimenezi pamene analankhula mawu amulemba la lerowa ndipo anawonjeranso kuti: “Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” Ulosiwu ukukwaniritsidwa masiku otsiriza ano moti pali mayiko ambiri padziko lapansi amene chiwerengero cha anthu ake n’chochepa poyerekezera ndi cha Mboni za Yehova padziko lonse. w16.06 4:1, 2
Lachisanu, March 9
Inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?—Mat. 6:26.
Yesu ankaona kuti Atate wake wakumwamba sangapatse chakudya mbalame koma n’kulephera kupatsa anthu zofunika pa moyo. (1 Pet. 5:6, 7) Koma nafenso sitingayembekezere kuti aziika chakudya pakamwa pathu. M’malomwake amatithandiza kuti tithe kulima chakudya kapena tipeze ndalama zoti tigulire chakudya cha tsiku ndi tsiku. Pa nthawi ya mavuto, angapangitse kuti anthu ena atithandize. Ngakhale kuti Yesu sanatchule zoti Yehova amapatsa mbalame malo okhala, iye amazipatsa nzeru, luso komanso zinthu zoti zithe kumangira zisa n’kumakhalamo. Ifenso Yehova angatithandize kuti tipeze malo okhala. Yesu ankadziwanso kuti pakapita nthawi apereka moyo wake kuwombola anthuwo. (Yerekezerani ndi Luka 12:6, 7.) Yesu anafera anthu n’cholinga choti adzapeze moyo wosatha.—Mat. 20:28. w16.07 1:11-13
Loweruka, March 10
Uchimo usakhale mbuye kwa inu, chifukwa simuli pansi pa chilamulo koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu.—Aroma 6:14.
Kodi uchimo ndi imfa zinayamba bwanji? Baibulo limati: “Chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo [Adamu] imfa inalamulira monga mfumu.” (Aroma 5:12, 14, 17) Uchimowu ukulamulira ana onse a Adamu ndipo umachititsa kuti tizifa. Komabe tingathe kusankha kuti uchimo usamatilamulire. Tikamakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu timayamba kulamuliridwa ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. (Aroma 5:20, 21) Ngakhale kuti ndife ochimwa, sitiyenera kulola kuti uchimo uzitilamulira. Koma tikachimwa mwangozi tizipempha Yehova kuti atikhululukire. Kodi chimachitika n’chiyani tikamalamuliridwa ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu? Paulo ananena kuti ‘kukoma mtima kwake kwakukulu kwatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.’—Tito 2:11, 12. w16.07 3:5, 6
Lamlungu, March 11
[Mulungu] anamubweretsa kwa iye.—Gen. 2:22.
Koma Adamu ndi Hava analephera kumvera Yehova ndipo banja lawo linayamba kukumana ndi mavuto. Zomwe zinachitika n’zakuti Satana Mdyerekezi, yemwe amatchedwanso “njoka yakale ija,” anapusitsa Hava pomuuza kuti adye chipatso cha “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Anamuuza kuti akadya, akhala ndi nzeru zapadera moti azitha kusiyanitsa yekha chabwino ndi choipa. Hava anachita zinthu mopanda ulemu chifukwa sanafunse kaye mwamuna wake za nkhaniyo. Nayenso Adamu m’malo momvera Mulungu anangolandira chipatso chimene Hava anamupatsa, n’kudya. (Chiv. 12:9; Gen. 2:9, 16, 17; 3:1-6) Mulungu atafunsa za nkhaniyi, Adamu anaimba mlandu mkazi wake. Nayenso Hava ananena kuti njoka ndi imene inamulakwitsa. (Gen. 3:12, 13) Zifukwa zimene ankaperekazi zinali zosamveka. Kusamvera kwawoku kunasonyeza kuti akuderera Yehova ndipo sankafuna kuti aziwalamulira. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kuti banja likhale losangalala, aliyense ayenera kumvera Yehova komanso kuvomereza zimene walakwitsa. w16.08 1:1, 4, 5
Lolemba, March 12
Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.—Mat. 19:6.
Mavuto ena a m’banja amayamba chifukwa choti zimene anthuwo ankayembekezera sizikuchitika. Mwachitsanzo, amaganiza kuti adzakhala ndi banja losangalala. Ndiyeno zikakhala kuti sizikuyenda, amakhumudwa n’kuona kuti agwiritsidwa mwala. Mavuto ena amabwera chifukwa choti mwamuna ndi mkazi amasiyana mmene amaonera zinthu komanso kumene anakulira. Mavuto angabwerenso chifukwa cha nkhani zokhudza ndalama, achibale komanso kulera ana. Koma n’zolimbikitsa kuti mabanja ambiri a Mboni za Yehova amapeza njira zabwino zothetsera mavutowa chifukwa amalola kuti Mulungu aziwatsogolera. Abale ndi alongo amene ali ndi mavuto aakulu a m’banja ayenera kuuza akulu. Akuluwa angawathandize kuti azigwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pothetsa mavutowo. Pamafunikanso kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera kuti uzitithandiza kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso kusonyeza makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa.—Agal. 5:22, 23. w16.08 2:11-13
Lachiwiri, March 13
Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.—Luka 5:10.
Yesu anali ndi nthawi yochepa yoti alalikire padzikoli. Koma ankayesetsa kupeza nthawi yolimbikitsa anthu amene asonyeza chidwi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anaphunzitsa anthu ali m’boti. Kenako anathandiza Petulo kugwira nsomba zambiri m’njira yodabwitsa. Ndiyeno ananena mawu amulemba la lerowa. Kodi zimene Yesu anachita komanso kulankhula zinathandiza bwanji anthu ena? Petulo ndi anzake atangofika kumtunda, “anasiya chilichonse ndi kumutsatira.” (Luka 5:1-11) Mfarisi wina amene ankaweruza m’Khoti Lalikulu la Ayuda dzina lake Nikodemo, ankafuna kudziwa zimene Yesu ankaphunzitsa. Koma ankaopa zimene anthu ena anganene akamuona akulankhula ndi Yesuyo. Choncho anapita kwa Yesu usiku ndipo iye sanadandaule kuti wamusokoneza. (Yoh. 3:1, 2) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yesu ankapeza nthawi yoti alimbitse chikhulupiriro cha anthu ena. Nafenso tiziyesetsa kuchita maulendo obwereza komanso kuphunzitsa anthu. w16.08 4:10, 11
Lachitatu, March 14
Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.—Mika 6:8.
Tiyenera kudzifufuza kuti tione ngati zimene timasankha pa nkhani ya zovala zimagwirizana ndi mfundo za Yehova. Tikatero timasonyeza kuti ndife odzichepetsa komanso tikufuna kuti Yehova azititsogolera. Munthu wodzichepetsa amaganiziranso ena komanso amapewa kuwaweruza. Choncho tiyeni tipitirize kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wathu potsatira mfundo zake zapamwamba komanso kulemekeza maganizo a anthu ena. Tiyeni tiziyesetsa kuvala zovala zimene zingathandize anthu kudziwa kuti ndife anthu a Mulungu. Akhristu anzathu komanso anthu ena azitha kuona kuti tikuimiradi Yehova Mulungu wathu. Tikamayesetsa kutsatira mfundo zake zapamwamba timasangalala kwambiri. Tikuyamikira kwambiri abale ndi alongo amene kavalidwe ndi khalidwe lawo labwino, zathandiza kuti anthu a maganizo abwino amvetsere uthenga wa Baibulo. Izi zimalemekezanso Yehova ndipo zimasangalatsa mtima wake. w16.09 3:18-20
Lachinayi, March 15
Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo potsirizira pake wapambana.—Gen. 32:28.
Yakobo anali wakhama ndipo sankafuna kuti chilichonse chimulepheretse kupeza madalitso ndipo anapezadi madalitsowo. (Gen. 32:24-26) Anapatsidwa dzina lomuyenerera lakuti Isiraeli, (kutanthauza “Mulungu Walimbana Naye,” kapena “Walimbana ndi Mulungu”). Zimene anachitazi zinachititsanso kuti Yehova azisangalala naye. Ifenso tizichita zonse zimene tingathe kuti Yehova asangalale nafe komanso atidalitse. Rakele yemwe anali mkazi wa Yakobo, ankafunitsitsa kuona mmene Yehova adzakwaniritsire lonjezo loti adzadalitsa mbewu ya mwamuna wake. Koma analibe ana. Pa nthawiyo, kukhala opanda mwana kunali kowawa kwambiri. Ndipotu palibe chimene Rakele akanachita kuti athetse vuto lakeli. Kodi iye anapeza bwanji mphamvu kuti apitirize kupirira? Rakele sanataye mtima m’malomwake anapitirizabe kupemphera mochokera pansi pa mtima. Yehova anayankha mapemphero akewo ndipo anamudalitsa pomupatsa ana.—Gen. 30:8, 20-24. w16.09 2:6, 7
Lachisanu, March 16
Pakuti mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.—Aheb. 4:12.
Makolo ayeneranso kuthandiza ana kuti azindikire ubwino wa mfundo za m’Baibulo. (Sal. 1:1-3) Mwachitsanzo, angauze ana awo kuti: ‘Tiyerekeze kuti mukupita pachilumba penapake ndiye mukusankha anthu oti mukakhale nawo. Kuti muzikakhala mwamtendere, kodi mungasankhe anthu otani?’ Kenako mungakambirane nawo malangizo abwino amene ali pa Agalatiya 5:19-23. Izi zingathandize anawo kumvetsa mfundo ziwiri. Yoyamba, mfundo za Mulungu zimathandiza kuti anthu azikhala mwamtendere komanso mogwirizana. Yachiwiri, Yehova akutiphunzitsa kuti tikonzekere moyo wa m’dziko latsopano. (Yes. 54:13; Yoh. 17:3) Ndiyeno kuti amvetse mfundozi, mungawapatse chitsanzo cha m’mabuku kapena magazini athu. Mwina mungasankhe nkhani ya munthu wina mu Nsanja ya Olonda pamutu wakuti, “Baibulo Limasintha Anthu.” w16.09 5:13, 14
Loweruka, March 17
Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu chifukwa masikuwa ndi oipa.—Aef. 5:16.
Ngakhale kuti timatanganidwa tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizipeza nthawi yophunzira patokha ndiponso yochita kulambira kwa pabanja. (Aef. 5:15) Cholinga chathu chisamakhale choti timalize masamba ambiri kapena tingopeza zoti tikayankhe pamisonkhano. Koma tiziyesetsa kuti Mawu a Mulungu azitifika pamtima ndiponso azitithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tisamangoganizira zimene tingachite kuti tithandize ena. Tiyenera kuganiziranso zoyenera kuchita kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. (Afil. 1:9, 10) Tizidziwa kuti tikamakonzekera utumiki, misonkhano kapena nkhani, nthawi zambiri timangoganizira mmene mfundozo zingathandizire anthu ena osati ifeyo. Mwachitsanzo, munthu amene amaphika, amalawa zakudyazo asanazipereke kwa anthu ena. Koma sikuti iyeyo amangodalira zimene amalawazo. Kuti thupi lake lisafooke, amayenera kudya chakudya chopatsa thanzi. Ifenso tiziyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu m’njira yoti azitifika pamtima n’cholinga choti tilimbitse chikhulupiriro chathu. w16.10 2:10, 11
Lamlungu, March 18
Mwa chikhulupiriro, timazindikira kuti mwa mawu a Mulungu, nthawi zosiyanasiyana anaziika m’malo mwake, moti zimene zikuoneka zatuluka m’zinthu zosaoneka.—Aheb. 11:3.
Baibulo limafotokoza tanthauzo la chikhulupiriro pa Aheberi 11:1. Limati chikhulupiriro ndi: (1) “Chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.” Izi ndi zinthu zimene Mulungu walonjeza koma panopa sizinachitike. Mwachitsanzo, walonjeza kuti adzathetsa zoipa zonse n’kubweretsa dziko latsopano. (2) “Umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” Palembali mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “umboni wooneka” akutanthauza “umboni wokhutiritsa” wa zinthu zoti sitingathe kuziona, koma zilipo. Mwachitsanzo, timakhulupirira zoti kuli Yehova Mulungu, Yesu Khristu, angelo komanso Ufumu wakumwamba. Ndiyeno kodi tingasonyeze bwanji kuti timayembekezera komanso kukhulupirira zinthu zosaoneka zomwe zafotokozedwa m’Mawu a Mulungu? Zochita ndi zolankhula zathu ndi zimene zingasonyeze. w16.10 4:6
Lolemba, March 19
Pitirizani kudandaulirana [kulimbikitsana].—Aheb. 3:13.
Yehova ndi Yesu amayamikira zimene timachita pothandiza kuti zinthu zokhudza Ufumu ziziyenda bwino. Iwo amaona kuti zimene tachita kapena kupereka ndi zamtengo wapatali ngakhale zitakhala zochepa. (Luka 21:1-4; 2 Akor. 8:12) Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena achikulire amachita khama kwambiri kuti azipezeka pamisonkhano komanso kupita mu utumiki nthawi zonse. Tiyenera kumayamikira komanso kulimbikitsa abale ndi alongowa. Tikaona kuti munthu wachita chinachake choyenera kumuyamikira, tisangokhala chete. Taganizirani zimene zinachitika Paulo ndi Baranaba ali ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Atsogoleri a sunagoge anawauza kuti: “Amuna inu, abale athu, ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.” Zitatero Paulo anakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri. (Mac. 13:13-16, 42-44) Choncho tikaona kuti tingathe kuuza munthu wina mawu olimbikitsa, tisamazengereze. Ndipotu tikakhala ndi chizolowezi cholimbikitsa ena, nafenso anthu azitilimbikitsa.—Luka 6:38. w16.11 1:3, 15, 16
Lachiwiri, March 20
Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.—Miy. 15:3.
Ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu la Yehova ndiponso kudziwa zimene amafuna kuti tizichita. Koma tilinso ndi udindo wochita zoyenera komanso kusonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Panopa makhalidwe a anthu akuipiraipirabe choncho tiyenera kuyesetsa ‘kudana ndi zoipa’ ngati mmene Yehova amachitira. (Sal. 97:10) Timapewa maganizo a anthu oipa amene amaona kuti “chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino.” (Yes. 5:20) Popeza timafuna kusangalatsa Yehova, timayesetsa kukhala aukhondo, kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kupewa chilichonse chimene chingakhumudwitse Mulungu. (1 Akor. 6:9-11) Timakonda kwambiri Yehova komanso timamudalira ndi mtima wonse. Choncho timatsatira mfundo za m’Mawu ake n’cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa iye. Timayesetsa kutsatira mfundozi kulikonse kaya ndi kunyumba, mumpingo, kuntchito kapena kusukulu. w16.11 3:13
Lachitatu, March 21
Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.—Aroma 13:1.
Sikuti zonse zimene Ophunzira Baibulo anachita pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse zinali zogwirizana ndi Malemba. Chifukwa chosamvetsa bwino Malemba, iwo sankadziwa zoyenera kuchita pa nkhani yogonjera maboma. Choncho nthawi zina ankachita nawo zinthu zokhudza nkhondo. Mwachitsanzo, pulezidenti wa ku United States atalamula kuti pa May 30, 1918 likhale tsiku lopempherera mtendere, Nsanja ya Olonda inalimbikitsa Ophunzira Baibulo kuti achite nawo mapempherowo. Abale ena anapereka ndalama zothandiza pa nkhondo ndipo ena mpaka anakhala asilikali n’kupita ku nkhondo. Ngakhale kuti abalewa ankalakwitsa zinthu zina, sitiyenera kuganiza kuti izi zinachititsa kuti Yehova awalange powapititsa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Mfundo ndi yoti Ophunzira Baibulo anayesetsa kuti asakhale mbali ya chipembedzo chonyenga ndipo pa nthawi ya nkhondo yapadziko lonse anali atangotsala pang’ono kutulukiratu mu ukapolowu.—Luka 12:47, 48. w16.11 5:9
Lachinayi, March 22
Tikuyenda motsatira za mzimu, osati motsatira zofuna za thupi.—Aroma 8:4.
Mwina mungadabwe kuti, n’chifukwa chiyani Paulo anachenjeza Akhristu odzozedwa kuopsa koyenda “mogwirizana ndi thupi”? Chenjezo limeneli ndi lofunika kwa Akhristu onse. Tikutero chifukwa Mkhristu aliyense atapanda kusamala angayambe kuyenda mongotsatira zilakolako za thupi. Mwachitsanzo, Paulo analemba kuti Akhristu ena a ku Roma anali akapolo a chiwerewere, kudya, kumwa ndi zinthu zina. Ena ankapusitsa “anthu oona mtima.” (Aroma 16:17, 18; Afil. 3:18, 19; Yuda 4, 8, 12) Munthu winanso wa ku Korinto anatengana ndi “mkazi wa bambo ake.” (1 Akor. 5:1) Ndiye m’pake kuti Mulungu anauzira Paulo kuti achenjeze Akhristu pa nkhani ya “kuika maganizo pa zinthu za thupi.” (Aroma 8:5, 6) Chenjezo limeneli ndi lofunikanso kwambiri masiku ano. w16.12 2:5, 8, 9
Lachisanu, March 23
Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.—Miy. 12:25.
Kufotokozera mavuto anu munthu wodalirika kungakuthandizeni kuchepetsa nkhawa. Mungafotokozere mwamuna kapena mkazi wanu, mnzanu wapamtima kapena mkulu mumpingo. Mukafotokozera mnzanu momasuka, mumayamba kumvetsa zinthu n’kuona zimene mungachite. Baibulo limanena kuti: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.” (Miy. 15:22) Yehova amagwiritsanso ntchito misonkhano yampingo potithandiza kuti tisamade nkhawa. Kumisonkhano timakumana ndi abale ndi alongo amene amatikonda komanso ‘timalimbikitsana’ nawo. (Aroma 1:12; Aheb. 10:24) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri. w16.12 3:17, 18
Loweruka, March 24
Hana . . . anayamba kupemphera kwa Yehova.—1 Sam. 1:10.
Ngati tikudwala kapena tili ndi vuto linalake limene sitingalithetse patokha, tiyenera kutulira Yehova nkhawa zathu n’kumakhulupirira kuti atithandiza. (1 Pet. 5:6, 7) Ndiponso tiziyesetsa kuchita zomwe tingathe kuti tizipindula ndi misonkhano komanso zonse zimene Yehova amatipatsa. (Aheb. 10:24, 25) Kodi makolo amene ana awo asiya kutumikira Yehova angaphunzire chiyani kwa Samueli? Iye sakanatha kuumiriza ana ake kuti azitsatira mfundo za Yehova zimene anawaphunzitsa. (1 Sam. 8:1-3) Choncho anangosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Koma Samueli anayesetsa kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ndipo ankachita zokondweretsa mtima wake. (Miy. 27:11) Masiku ano makolo ambiri achikhristu amakumananso ndi vuto ngati lomweli. Koma amakhulupirira kuti Yehova ndi wokonzeka kulandiranso olakwa omwe alapa mofanana ndi bambo wa mu fanizo la Yesu la mwana wolowerera. (Luka 15:20) Makolo amenewa amayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ndipo amadziwa kuti chitsanzo chawo chingathandize ana awowo kuti abwerere. w17.01 1:15, 16
Lamlungu, March 25
[Muzichita zinthu] modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.
Munthu wodzichepetsa amazindikira zimene sayenera kuchita ndipo akalakwitsa amavomereza kulakwa kwake. Iye amamvetsera maganizo a ena ndipo amaphunzirapo kanthu. Choncho munthu wodzichepetsa amasangalatsa kwambiri Yehova. Munthu wodzichepetsa amazindikiranso kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita. Iye amadziwanso zinthu zimene si udindo wake kuchita. Zimenezi zimamuthandiza kuti azilemekeza ena komanso aziwachitira zinthu mokoma mtima. Koma mosazindikira munthu angayambe kuganiza kapena kuchita zinthu modzikuza. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Mwina tingayambe kudziona kuti ndife ofunika kuposa ena chifukwa choti tili ndi udindo winawake. (Aroma 12:16) Kapena tingayambe kuchita zinthu modzitama kuti anthu atione. (1 Tim. 2:9, 10) Mwinanso tingayambe kugwiritsa ntchito udindo wathu, kapena zinthu zina pofuna kuti anthu aziyendera maganizo athu.—1 Akor. 4:6. w17.01 3:6-8
Lolemba, March 26
Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo, ndipo ulemerero wa anthu okalamba ndiwo imvi zawo.—Miy. 20:29.
Panopa, ntchito m’gulu la Yehova yakula kwambiri ndipo ikufuna zambiri. Ntchito zatsopano zachititsa kuti papezeke njira zatsopano zogwirira ntchitozo ndipo njira zambiri ndi zamakono. Ndiyeno achikulire ena amavutika kuzolowera njira zatsopanozo. (Luka 5:39) Ngakhale zitakhala kuti achikulirewo sakuvutika, achinyamata amakhala ndi mphamvu zambiri. Choncho ndi bwino kuti achikulire aziphunzitsa achinyamata kuti akhale ndi maudindo akuluakulu. (Sal. 71:18) Akhristu ena amene ali ndi maudindo zimawavuta kuphunzitsa achinyamata. Ena amaopa kuti alandidwa udindo umene amaukonda kapena amakayikira achinyamatawo kuti sangachite bwino zinthu. Ndiye pali enanso amene amaganiza kuti alibe nthawi yophunzitsa ena. Koma nawonso abale achinyamata ayenera kukhala odekha akaona kuti sakupatsidwa udindo winawake. w17.01 5:3, 4
Lachiwiri, March 27
Mwa kuchita chinthu chimodzi cholungamitsa, anthu kaya akhale amtundu wotani akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.—Aroma 5:18.
Yesu anali wangwiro ngati mmene Adamu analili. (Yoh. 1:14) Koma mosiyana ndi Adamu, Yesu anamvera Yehova. Ngakhale pamene anakumana ndi mayesero aakulu, iye sanachimwe kapena kuphwanya malamulo a Mulungu. Popeza Yesu anali wangwiro, anapulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa powafera. Adamu anali wangwiro ndipo akanatha kukhala wokhulupirika komanso womvera. Choncho dipo la Yesu linali lokwanira ndendende zimene Adamu anataya. (1 Tim. 2:6) Iye anakhala nsembe ya dipo imene inathandiza kuti “anthu ambiri,” kaya amuna, akazi komanso ana, adzapeze moyo wosatha. (Mat. 20:28) Dipoli ndi limene linatsegula njira yoti cholinga choyambirira cha Mulungu chidzakwaniritsidwe. (2 Akor. 1:19, 20) Dipo limathandiza kuti anthu onse okhulupirika adzapeze moyo wosatha. w17.02 1:15, 16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Yohane 12:12-19; Maliko 11:1-11
Lachitatu, March 28
Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo.—Aheb. 12:2.
Tiyerekezere kuti muli pakati pa mtsinje waukulu ndipo mukayang’ana kutsogolo mukuona kuti padakali mtunda wautali kuti mukafike kutsidya. Mavuto amene timakumana nawo angafanane ndi zimenezi. Yesu atakumana ndi mavuto anamvanso chimodzimodzi. Iye ananyozedwa komanso anamva ululu kwambiri atakhomeredwa pamtengo. (Aheb. 12:3) Koma kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Iye ankaganizira madalitso amene adzapeze akapirira. Ankaona kuti kupirira kwake kuthandiza kuti dzina la Yehova liyeretsedwe komanso kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Ankadziwanso kuti mavutowo ndi akanthawi koma madalitso amene adzapeze ndi amuyaya. Masiku anonso tingakumane ndi mavuto aakulu koma tizikumbukira kuti mavutowa ndi akanthawi. w16.04 2:10
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Yohane 12:20-50
Lachinayi, March 29
Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa machimo athu.—Aef. 1:7.
M’dzikoli anthu akachimwa sadandaula chilichonse moti ambiri sadziwa n’komwe kuti akufunika kupulumutsidwa. Ena sadziwanso kuti uchimo n’chiyani, umatikhudza bwanji komanso tingatani kuti tisakhale akapolo ake. Anthu amene amamvetsera uthenga wathu amasangalala akadziwa kuti Yehova amatikonda ndipo anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu potumiza Mwana wake kuti adzapereke dipo lotiwombola. (1 Yoh. 4:9, 10) Nsembe ya dipo imasonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri ndiponso kukoma mtima kwake ndi kwakukulu kwabasi. N’zosangalatsa kudziwa kuti tikakhulupirira nsembeyi, machimo athu amakhululukidwa ndipo sitidziimba mlandu. (Aheb. 9:14) Umenewutu ndi uthenga wabwino wofunika kuuza anthu ena. w16.07 4:6, 7
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Luka 21:1-36
Lachisanu, March 30
[Khristu] anatilanditsa kwamuyaya.—Aheb. 9:12.
Tikamakhulupirira dipo machimo athu onse akhoza kukhululukidwa. Paja Mawu a Mulungu amanena kuti machimo athu angathe kufafanizidwa. (Mac. 3:19-21) Monga tanenera kale, dipo limathandiza kuti Yehova aziona kuti odzozedwa ndi ana ake. (Aroma 8:15-17) Ngati ndife a “nkhosa zina” tingati Yehova walemba kale chikalata chokhala ndi dzina lathu chotilola kuti tikhale ana ake. Ndiyeno tikadzakhala angwiro n’kupambana mayesero omaliza, iye adzasainira chikalatacho n’kutitenga kuti tikhale ana ake apadzikoli. (Aroma 8:20, 21; Chiv. 20:7-9) Yehova sadzasiya kukonda ana ake ndipo madalitso amene adzawapatse chifukwa cha dipo adzakhala osatha. Mphatso ya dipo ndi yosafwifwa ndipo palibe amene angatilande. w17.02 2:15, 16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6
Tsiku la Chikumbutso
Dzuwa Litalowa
Loweruka, March 31
Wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.—1 Yoh. 2:1.
Pamene Yehova ankatikoka kuti tikhale naye pa ubwenzi, ankadziwa kuti tizilakwitsa zinthu zina. Popeza Mulungu amatidziwa bwino komanso amadziwa zimene zili mumtima mwathu, ayeneranso kuti ankadziwa zinthu zimene zidzativute kusintha. Ankadziwanso kuti nthawi zina tingachite tchimo. Komabe zimenezi sizinamulepheretse kuti atikoke kukhala anzake. Mulungu amatikonda kwambiri ndipo anatipatsa mphatso yamtengo wapatali. Iye anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake ngati nsembe ya dipo. (Yoh. 3:16) Tikalakwa n’kupempha kuti Yehova atikhululukire, amagwiritsa ntchito nsembe imeneyi ndipo tingathe kukhalabe naye pa ubwenzi ngakhale kuti timalakwitsa zinthu zina.—1 Tim. 1:15. w16.05 4:6, 7
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Mateyu 26:17-19; Maliko 14:12-16; Luka 22:7-13 (Zochitika dzuwa litalowa pa Nisani 14) Yohane 13:1-5; 14:1-3