April
Lamlungu, April 1
Inu amene kale munali otalikirana naye ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa, tsopano wagwirizana nanunso pogwiritsa ntchito thupi lanyama la mwanayo kudzera mu imfa yake.—Akol. 1:21, 22.
Tiyenera kuuza anthu kuti ali ndi mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Mlengi wathu. Anthu amene sanayambe kukhulupirira nsembe ya Yesu amakhala adani a Mulungu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) N’zosangalatsa kuti nsembe ya Khristu imatithandiza kuti tigwirizanenso ndi Mulungu. (2 Akor. 5:18-20) Ifeyo timagwira kwambiri ntchito yophunzitsa anthu n’kumawathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Zimene timachitazi n’zofunika kwambiri pa ntchito yolalikira. w16.07 4:8-10
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Yohane 19:1-42
Lolemba, April 2
Dzina lanu liyeretsedwe.—Mat. 6:9.
Yesu anayamba pemphero lachitsanzo ndi mfundo yoti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Dzinali limasonyeza kuti Mulungu ndi wabwino, wamkulu komanso woyera kwambiri. Popeza Yehova ndi woyera, mfundo zake ndi malamulo ake nazonso n’zoyera. Ngakhale zili choncho, m’munda wa Edeni, Satana anatsutsa zoti Mulungu ndi woyenera kupereka malamulo oti anthu azitsatira. Ponena zabodza zokhudza Yehova, Satana anadetsa dzina loyera la Mulungu. (Gen. 3:1-5) Koma Yesu ankakonda kwambiri dzina la Yehova. (Yoh. 17:25, 26) Iye anathandiza kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. (Sal. 40:8-10) Ali padzikoli sanalakwitse chilichonse ndipo anasonyeza kuti Yehova ndi woyenera kupereka malamulo oti anthu ndi angelo azitsatira. Kukhulupirika kwa Yesu mpaka imfa kunasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kumvera bwinobwino malamulo a Mulungu. w17.02 2:2-4
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66 (Zochitika pa Nisani 16 Dzuwa litalowa) Yohane 20:1
Lachiwiri, April 3
Mwanawankhosa alandire ulemu [ndi] ulemerero.—Chiv. 5:13.
Mwanawankhosa ndi Yesu Khristu ndipo iye ndi “amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yoh. 1:29) Baibulo limasonyeza kuti Yesu ndi wapamwamba kuposa mafumu onse. Limati iye ndi “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye, adzaonekera pa nthawi zake zoikidwiratu. Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, amene amakhala m’kuwala kosafikirika. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.” (1 Tim. 6:14-16) Angelo amalengeza kuti: “Mwanawankhosa amene anaphedwa ndiye woyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero, ndi madalitso.” (Chiv. 5:12) Kulemekeza Yehova ndi Khristu si nkhani yochita kusankha. Kuti tidzapeze moyo wosatha tiyenera kuchita zimenezi basi.—Sal. 2:11, 12; Yoh. 5:23. w17.03 1:3, 4
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Yohane 20:2-18
Lachitatu, April 4
Ngati mukunditenga . . . ndidzakhala mtsogoleri wanu!”—Ower. 11:9.
Iye ankadziwa bwino mbiri ya Aisiraeli ndipo ankazindikira zinthu zoyenera ndi zosayenera pamaso pa Yehova. (Ower. 11:12-27) Yefita akamasankha zochita ankatsatira mfundo za m’Chilamulo. Ankadziwa kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azikondana osati kusungirana zifukwa. Chilamulo chinkanena kuti munthu ayenera kuthandiza anzake ngakhalenso anthu amene amadana naye. (Eks. 23:5; Lev. 19:17, 18) Yefita ayenera kuti ankaganizira chitsanzo cha anthu ngati Yosefe. Paja Yosefe anathandiza abale ake ngakhale kuti ‘ankadana naye.’ (Gen. 37:4; 45:4, 5) Kuganizira zimenezi kunathandiza Yefita kuti achite zinthu zosangalatsa Yehova. Zimene abale ake anamuchitira ziyenera kuti zinamuwawa kwambiri, komabe sizinamulepheretse kutumikira Yehova komanso anthu ake.—Ower. 11:1-3. w16.04 1:8, 9
Lachinayi, April 5
Tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi mogwirizana.—Mac. 2:46.
Kuyambira kale atumiki a Yehova amaona kuti kusonkhana n’kofunika. Mwachitsanzo, mpingo wachikhristu utangokhazikitsidwa, Akhristu “anali kusonkhana kukachisi” tsiku ndi tsiku. Inunso muyenera kuti mumaona kuti kusonkhana ndi abale ndi alongo athu n’kofunika kwambiri. Komabe Akhristu onse amakumana ndi mavuto omwe angawalepheretse kusonkhana. Zinthu monga ntchito, kutanganidwa komanso kutopa chifukwa cha zimene timachita tsiku ndi tsiku, zingapangitse kuti tizivutika kupita kumisonkhano. Koma kukumbukira kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri kungatithandize kuti tisanajombe. Ena amavutika kupita kumisonkhano pa zifukwa monga matenda aakulu. Akulu angathandize kuti anthu amenewa azipindulabe ndi misonkhano kudzera pa foni kapena kumvetsera ikajambulidwa. w16.04 3:3
Lachisanu, April 6
Limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.—Yoh. 16:33.
Chinthu china chimene chingatithandize kuti tisalowerere ndale, ndi kutsanzira anthu ena okhulupirika. Nkhani zawo zingatithandize kuti tisagonje. Mwachitsanzo, Sadirake, Mesake ndi Abedinego anakana kulambira fano la ku Babulo. (Dan. 3:16-18) Nkhani zimenezi zathandiza abale ndi alongo ambiri kuti azilimba mtima n’kukana kulambira mbendera. Nayenso Yesu sankalowerera zochitika za m’dzikoli. Iye ankadziwa kuti chitsanzo chake chingathandize otsatira ake. Choncho anawauza kuti ‘alimbe mtima.’ Abale ndi alongo nawonso angakulimbikitseni ngati mutawafotokozera mavuto anuwo. Mungawapemphe kuti akupempherereni. Koma tisaiwale kuti nafenso tiyenera kupempherera abale athu komanso kuyesetsa kuwathandiza.—Mat. 7:12. w16.04 4:16, 18
Loweruka, April 7
Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa.—Sal. 110:3.
Kodi a Mboni za Yehova amatolera zopereka pa Nyumba ya Ufumu kapena pamisonkhano ikuluikulu? Ayi, ndalama zoyendetsera ntchito yawo ndi zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. (2 Akor. 9:7) M’chaka cha 2015 chokha, a Mboni za Yehova anathera maola pafupifupi 2 biliyoni akulalikira uthenga wabwino. Ankachititsanso maphunziro a Baibulo oposa 9 miliyoni mwezi uliwonse. Chochititsa chidwi n’choti iwo salipidwa komanso amagwiritsa ntchito ndalama zawo akamagwira ntchitoyi. Pofotokoza ntchito imene a Mboni za Yehova amagwira, wochita kafukufuku wina ananena kuti: “Cholinga chachikulu cha a Mboni ndi kulalikira komanso kuphunzitsa. . . . Alibe abusa amene amalipidwa ndipo izi zimapangitsa kuti asamawononge ndalama zambiri.” Ndiyeno kodi cholinga chathu chimakhala chotani tikamalalikira? Mwachidule tingati timalalikira chifukwa timakonda Yehova komanso anzathu. Zimenezi zimakwaniritsa ulosi wapalemba la leroli. w16.05 2:9
Lamlungu, April 8
Koma nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino.—Yak. 3:17.
Kuzindikira mfundoyi kungatithandize kuti tizipewa zosangalatsa zimene zingapangitse kuti tiziganizira kapena kuchita zoipa. Akhristu olimba mwauzimu sachita kufunsa ngati kuli koyenera kapena ayi kuwerenga buku, kuonera filimu kapena kuchita masewera amene Mulungu amadana nawo. Amadziwiratu maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Nthawi zina pamakhala njira zingapo zimene munthu angasankhe koma zonsezo zili zokondweretsa Yehova. Komabe pali nkhani zina zazikulu zimene tingafunike kupempha malangizo kwa akulu kapena Akhristu ena olimba mwauzimu. (Tito 2:3-5; Yak. 5:13-15) Koma sitiyenera kuwapempha kuti atisankhire zochita. Mkhristu aliyense ayenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mphamvu zake za kuzindikira. (Aheb. 5:14) Tizikumbukira zimene Paulo ananena. Paja iye anati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”—Agal. 6:5. w16.05 3:15, 16
Lolemba, April 9
Ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.—1 Tim. 1:13.
Yehova akafuna kusankha munthu woti amuumbe sayang’ana nkhope koma mtima. (1 Sam. 16:7b) Mfundoyi imaonekera bwino tikaona zimene anachita pamene ankakhazikitsa mpingo wachikhristu. Ena amene anawasankha ankaoneka ngati osayenera. (Yoh. 6:44) Chitsanzo ndi Mfarisi wina, dzina lake Saulo. Popeza Yehova “amayesa mitima” sanaone kuti Saulo sangatheke kuumbidwa. (Miy. 17:3) M’malomwake ankaona kuti akhoza kumuumba n’kukhala chiwiya cha mtengo wapatali “chochita kusankhidwa” kuti akachitire umboni “kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Mac. 9:15) Anthu ena omwe Mulungu ankawaona kuti ndi ‘ziwiya zolemekezeka’ poyamba anali oledzera, achiwerewere komanso akuba. (Aroma 9:21; 1 Akor. 6:9-11) Koma anthuwa ataphunzira za Mulungu n’kuyamba kumukhulupirira, analola kuti iye awaumbe. w16.06 1:4
Lachiwiri, April 10
Taonani! Mofanana ndi dongo limene lili m’manja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine.—Yer. 18:6.
Mulungu watipatsa zinthu monga Mawu ake, mpingo komanso ntchito yolalikira kuti zitithandize kukhala ngati dongo losavuta kuumbidwa. Madzi amathandiza kuti dongo lifewe bwino. Nafenso tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kuganizira kwambiri zimene tawerengazo, zimakhala zosavuta kuti Yehova atiumbe. Yehova anauza mafumu achiisiraeli kuti azikopera Chilamulo n’kumachiwerenga tsiku lililonse. (Deut. 17:18, 19) Nawonso atumwi ankadziwa kuti kuwerenga Malemba komanso kusinkhasinkha kunali kofunika kwambiri. Polemba Baibulo anagwira mawu Malemba Achiheberi kambirimbiri ndipo akamalalikira ankalimbikitsanso anthu kuchita chimodzimodzi. (Mac. 17:11) Nafenso timadziwa kuti kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse komanso kuganizira zimene tawerengazo n’kofunika kwambiri. (1 Tim. 4:15) Kuchita zimenezi kumatithandiza kuti tikhalebe odzichepetsa kuti Yehova apitirize kutiumba. w16.06 2:10
Lachitatu, April 11
Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.—Yoh. 13:35.
A Mboni za Yehova anasonyeza chikondi chimenechi pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Pa nthawiyi, anthu okwana 55 miliyoni anaphedwa. Koma a Mboni sanamenye nawo nkhondoyi. (Mika 4:1, 3) Zimenezi zinawathandiza kuti akhalebe ‘oyera pa mlandu wa magazi a anthu onse.’ (Mac. 20:26) Anthu a Mulungu akuwonjezeka ngakhale kuti akukhala m’dziko limene wolamulira wake ndi Satana. Baibulo limati iye ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4) Satana amagwiritsa ntchito anthu andale komanso ofalitsa nkhani kuti alepheretse ntchito yolalikira, koma zimenezi sizingatheke. Komabe podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa, Satana akuyesetsa kuchititsa anthu kuti asiye kulambira Mulungu ndipo akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana.—Chiv. 12:12. w16.06 4:3, 4
Lachinayi, April 12
Phunzirani pa mmene maluwa akutchire amakulira.—Mat. 6:28.
Tonsefe timafuna kutchena, makamaka tikamapita mu utumiki komanso kumisonkhano. Koma kodi tiyenera kuda nkhawa kwambiri “pa nkhani ya zovala”? Ayi. Tikutero chifukwa pa nkhani imeneyinso Yesu anatchula zimene Yehova amachita. Tingaphunzire zambiri tikaona mmene “maluwa akutchire” amaonekera. Mwina Yesu ankaganizira za maluwa osiyanasiyana amene amaoneka okongola kwambiri. Komatu palibe chilichonse chimene maluwa amenewa amachita kuti azioneka okongola chonchi. Koma Yesu ananena kuti “ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.” Kenako Yesu anafunsa anthuwo kuti: “Ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, . . . kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu?” (Mat. 6:29, 30) Yankho la funsoli linali lodziwikiratu. Koma ophunzira a Yesuwo anali ndi chikhulupiriro chochepa. (Mat. 8:26; 14:31; 16:8; 17:20) Choncho ankafunika kulimbitsa chikhulupiriro kuti azidalira kwambiri Yehova. Kodi ifeyo timakhulupirira kuti Yehova angathe kutipatsa zonse zomwe timafunikira? w16.07 1:15, 16
Lachisanu, April 13
Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana monga oyang’anira abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.—1 Pet. 4:10.
Yehova akhoza kutithandiza kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo. (1 Pet. 1:6) Nthawi zonse iye amatisonyeza kukoma mtima mogwirizana ndi vuto limene takumana nalolo. Yehova akatisonyeza kukoma mtima m’njira zosiyanasiyana, timapeza madalitso ambiri. Dalitso lina limene timapeza ndi loti Yehova amatikhululukira machimo athu chifukwa cha kukoma mtima kwake. Koma chofunika n’kulapa komanso kuyesetsa kulimbana ndi mtima wofuna kuchita machimo. (1 Yoh. 1:8, 9) Popeza Mulungu amatisonyeza chifundo chonchi, tiyenera kumuyamikira komanso kumulemekeza. Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Iye [Yehova] anatilanditsa ku ulamuliro wa mdima, n’kutisamutsira mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo, kutanthauza kuti machimo athu anakhululukidwa.” (Akol. 1:13, 14) Tikakhululukidwa machimo athu timapezanso madalitso ambirimbiri. w16.07 3:7-9
Loweruka, April 14
Idzaphwanya mutu wako.—Gen. 3:15.
Satana atayambitsa mavuto m’munda wa Edeni, Yehova ananena ulosi woyamba m’Baibulo wonena za tsogolo labwino la anthu. Malemba anasonyeza kuti Mulungu adzatumiza winawake yemwe adzaphwanye Mdyerekezi. Zimenezi zidzathandiza kuti anthu omvera apeze moyo wosatha mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu choyambirira. (Yoh. 3:16) Zimene Adamu ndi Hava anachita pokana ulamuliro wa Yehova zinayambitsa mavuto m’banja lawo komanso mabanja onse. Mwachitsanzo, zinachititsa kuti Hava ndiponso akazi ena onse azivutika akakhala oyembekezera komanso akamabereka. Zinachititsanso kuti akazi azikhumba amuna awo koma amunawo aziwapondereza ndi kuwachitira nkhanza ngati mmene zilili m’mabanja ambiri masiku ano. (Gen. 3:16) Koma Baibulo limalimbikitsa amuna kuti azikonda akazi awo. Limanenanso kuti akazi ayenera kugonjera amuna awo. (Aef. 5:33) Mwamuna ndi mkazi akakhala oopa Mulungu komanso ogwirizana, mavuto amachepa m’banja mwinanso kutheratu. w16.08 1:6, 7
Lamlungu, April 15
Mkaziwe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mwamuna wako? Kapena mwamunawe, ukudziwa bwanji, mwina ungapulumutse mkazi wako?—1 Akor. 7:16.
Pali Akhristu ena amene akazi kapena amuna awo si Mboni. Baibulo limalimbikitsa Akhristu oterewa kuti azikhalabe ndi mnzawoyo. (1 Akor. 7:12-14) Kaya akudziwa kapena ayi, munthu yemwe si Mboniyo “amayeretsedwa” chifukwa chokhala pa banja ndi wa Mboni. Komanso Mulungu amaona kuti ana a m’banjali ndi “oyera” ndipo angakhale naye pa ubwenzi. Pafupifupi mumpingo uliwonse muli mabanja amene poyamba wa Mboni anali mmodzi ndipo anathandiza kuti mnzakeyo ayambe kulambira Yehova. Mtumwi Petulo anapereka malangizo othandiza kwa akazi achikhristu omwe amuna awo si Mboni. Iye anati: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”—1 Pet. 3:1-4. w16.08 2:14, 15
Lolemba, April 16
Kondanani kwambiri kuchokera mumtima.—1 Pet. 1:22.
Yehova amafuna kuti anthu ake azikondana komanso kuthandizana. (Luka 22:24-27) Mwana wa Mulungu ankatumikira anthu ndi mtima wonse mpaka anawafera. (Mat. 20:28) Komanso Dorika ankachita “ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.” (Mac. 9:36, 39) Panalinso mlongo wina wa ku Roma dzina lake Mariya, amene ‘ankachita ntchito zambiri’ pothandiza anthu amumpingo wawo. (Aroma 16:6) Ndiye kodi tingaphunzitse bwanji atsopano kuti adziwe ubwino wothandiza abale ndi alongo awo? Akhristu angatenge atsopano pamene akupita kukaona odwala komanso okalamba. Nthawi zinanso makolo angatenge ana awo pa maulendo oterewa. Akulu angathandizane ndi Akhristu ena poonetsetsa kuti abale ndi alongo achikulire ali ndi chakudya komanso malo okhala abwino. Zonsezi zingathandize kuti ana komanso atsopano aphunzire kuchitira ena chifundo. Zingawathandizenso kudziwa kuti akulu amakonda anthu onse amumpingo.—Aroma 12:10. w16.08 4:13, 14
Lachiwiri, April 17
Mbewu zimene zafesedwa panthaka yabwino, ndi munthu amene wamva mawu ndi kuzindikira tanthauzo lake, amene amabaladi zipatso.—Mat. 13:23.
Mtsikana wina wa Mboni wa ku France anati: “Aphunzitsi a kusukulu kwathu amadabwa akamva kuti pali ana ena amene amakhulupirirabe Baibulo.” Masiku ano anthu ambiri sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Ngati ndinu wachinyamata wa Mboni kapena mukuphunzira Baibulo, mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingamutsimikizire bwanji munthu kuti kuli Mlengi?’ Akhristufe timalimbikitsidwa kuti tiziganizira kwambiri zimene tamva kapena kuwerenga, kuti tidziwe ngati zili zoona kapena ayi. Paja Baibulo limati: “Kuganiza bwino kudzakuyang’anira.” Kuganiza bwino kungakuthandizeni kuti muzikana mfundo zabodza komanso kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova. (Miy. 2:10-12) Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chenicheni amafunika kudziwa zolondola zokhudza Mulungu. (1 Tim. 2:4) Choncho mukamaphunzira Baibulo kapena mabuku athu, musamathamange. Muzigwiritsa ntchito luso lanu la kuganiza kuti muzindikire “tanthauzo” la zimene mukuwerengazo. w16.09 4:1-3
Lachitatu, April 18
Pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.—Aroma 12:21.
N’kutheka kuti tinakula movutika kapena panopa tikukumana ndi mavuto enaake. Komabe tiyenera kupitiriza kulimbana ndi mavuto athuwo. Tizikhulupirira kuti tikachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa. (Gen. 39:21-23) Kodi nanunso mukukumana ndi vuto linalake? Mwina anthu ena akukuchitirani zinthu zopanda chilungamo, kukusalani kapena kukunyozani. Mwinanso munthu wina anakunamizirani zinazake chifukwa cha nsanje. M’malo mofooka, mungachite bwino kuganizira zimene zinathandiza Yakobo, Rakele ndi Yosefe kuti apitirizebe kutumikira Yehova mosangalala. Mulungu anawathandiza komanso kuwadalitsa chifukwa ankakonda zinthu zauzimu. Iwo sanafooke ndipo ankachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero awo. Popeza tili kumapeto kwenikweni kwa dziko loipali, tiyenera kuyesetsa kuti tisafooke n’cholinga choti tidzapeze madalitso amene Mulungu walonjeza. Kodi inuyo mukuyesetsa kuti Mulungu azisangalala nanu? w16.09 2:8, 9
Lachinayi, April 19
Koma makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo . . . chikhulupiriro.—Agal. 5:22.
Chitsanzo chabwino cha makolo chimathandiza kwambiri ana. Paja ana anu amaona kwambiri zimene mumachita. Choncho muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba. Ana anu aziona kuti mumadalira kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, makolo ena a ku Bermuda akakumana ndi mavuto, ankapemphera limodzi ndi ana awo kuti Yehova awatsogolere. Ankalimbikitsanso ana awowo kuti nawonso azipemphera paokha. Iwo anati: “Tinauzanso mwana wathu wamkazi kuti azidalira kwambiri Yehova, azichita khama pomutumikira ndiponso asamade nkhawa kwambiri.” Ataona zotsatira zake, anadziwa kuti Yehova akutithandiza. Zimenezi zinapangitsa kuti ayambe kumukhulupirira kwambiri komanso kukhulupirira Baibulo.” Komabe muzikumbukira kuti simungakakamize ana anu kuti akhale ndi chikhulupiriro. Ntchito yanu ndi yongodzala ndi kuthirira ndipo Mulungu ndi amene amakulitsa. (1 Akor. 3:6) Choncho muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera ndipo muzichita khama pophunzitsa ana anu. Mukamachita zimenezi, Mulungu adzakudalitsani kwambiri.—Aef. 6:4. w16.09 5:16-18
Lachisanu, April 20
[Uzikhomereza mawu awa] mwa ana ako.—Deut. 6:7.
M’bale wina dzina lake Serge ndi mkazi wake Muriel, omwe chilankhulo chawo ndi Chifulenchi anakhala kugawo la chilankhulo china kwa zaka zoposa zitatu. Kenako anazindikira kuti mwana wawo wazaka 17 sankasangalala kwenikweni ndi zinthu zokhudza kulambira. A Serge anafotokoza kuti: “Titazindikira za vutoli, tinaganiza zobwerera kumpingo wathu wakale.” Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse makolo kuganiza zobwerera kumpingo wa chilankhulo chimene ana awo amadziwa? Choyamba, ngati sakutha kupeza nthawi yokwanira komanso zinthu zimene zingawathandize pophunzitsa ana awo kukonda Yehova kwinaku akuwaphunzitsanso chilankhulo china. Chachiwiri, ngati akuona kuti anawo sakukonda kulalikira m’gawo la chilankhulo china kapena sakusangalala ndi zinthu zokhudza kulambira. Zikatere, kubwerera kumpingo wa chilankhulo chimene anawo amachidziwa bwino mpaka atalimba mwauzimu kungathandize kwambiri.—Deut. 6:5-7. w16.10 2:14, 15
Loweruka, April 21
Mwa chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa kuti banja lake lipulumukiremo.—Aheb. 11:7.
Anthu amene ankaona Nowa akumanga chingalawa ayenera kuti ankafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukumanga chingalawa chachikulu choncho? Kodi Nowa ankangokhala chete? Kapena kodi ankangowauza kuti sizikuwakhudza? Ayi. Popeza iye anali ndi chikhulupiriro, ankawalalikira molimba mtima komanso ankawachenjeza za chiweruzo cha Mulungu. Ayenera kuti ankawauza mawu amene Mulungu ananena akuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse, popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. . . . Ndidzabweretsa chigumula chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo m’thupi mwake. Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.” Choncho Nowa anasonyezanso kuti anali ndi chikhulupiriro pokhala “mlaliki wa chilungamo.”—Gen. 6:13, 17, 18; 2 Pet. 2:5. w16.10 4:7
Lamlungu, April 22
Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.—Yer. 10:23.
Makolo achikhristu amasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova akamaphunzitsa ana awo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Iwo salera ana mongotengera chikhalidwe cha kumene amakhala. Amayesetsanso kuti mzimu wa dziko usasokoneze banja lawo. (Aef. 2:2) Mwamuna wachikhristu sangaganize kuti, ‘Kwathu kuno udindo wophunzitsa ana ndi wa azimayi.’ Amakumbukira malangizo a m’Baibulo akuti: “Inunso abambo, . . . muwalere [ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Makolo achikhristu amafuna kuti ana awo akhale pa ubwenzi ndi Yehova ngati mmene Samueli anachitira ali wamng’ono. (1 Sam. 3:19) Si nzeru kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu zokhudza banja lathu popanda kufufuza malangizo a m’Baibulo. Paja anthufe sitingathe kuwongolera mapazi athu choncho timafunika kutsogoleredwa ndi Atate wathu wakumwamba. w16.11 3:14, 15
Lolemba, April 23
Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu, Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, Ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizira.—Sal. 8:3, 4.
Chilengedwe chimasonyeza kuti Mulungu ndi wadongosolo. Baibulo limati: “Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru. Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.” (Miy. 3:19) Anthufe timangodziwa “kambali kakang’ono chabe ka zochita za [Mulungu], ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Komabe zochepa zimene timadziwazi, zimatithandiza kuzindikira kuti mapulaneti, nyenyezi komanso milalang’amba zinapangidwa mwadongosolo kwambiri. Milalang’amba ili ndi nyenyezi mamiliyoni ambirimbiri koma zonse zimayenda mwadongosolo. Pulaneti iliyonse ili ndi malo amene imayenda mozungulira dzuwa ndipo zimakhala ngati mapulanetiwa akutsatira malamulo apamsewu. Zonsezi zimatheka chifukwa Yehova ndi amene anakonza zoti mapulaneti ndi nyenyezi ziziyenda mwadongosolo. Iye anapanga kumwamba ndi dziko lapansi “mwanzeru.” Choncho tiyenera kumutamanda, kumulambira komanso kukhala okhulupirika kwa iye.—Sal. 136:1, 5-9. w16.11 2:3
Lachiwiri, April 24
Pamene azidzapereka nsembe zawo ngati mphatso, Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka molungama.—Mal. 3:3.
Lemba la Malaki 3:1-3 limafotokoza zimene zinachitikira Ophunzira Baibulo kuyambira mu 1914 kufika kumayambiriro kwa 1919. Yehova Mulungu, yemwe ndi “Ambuye woona,” ndi Yesu Khristu, yemwe ndi “mthenga wa pangano,” analowa m’kachisi wauzimu kuti akayendere “ana a levi” omwe ndi odzozedwa. Yehova atayeretsa anthu akewa anaona kuti ndi oyenera kuwapatsa udindo wina. Ndiyeno mu 1919, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anaikidwa kuti azipereka chakudya chauzimu kwa atumiki a Mulungu. (Mat. 24:45) Apa tsopano anthu a Mulungu anamasulidwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. Kuyambira nthawi imeneyo, anthu a Yehova aphunzira zambiri ndipo akudziwa bwino cholinga cha Mulungu komanso amamukonda kwambiri. Iwo amayamikira madalitso amene Yehova akuwapatsa. w16.11 5:14
Lachitatu, April 25
“Ndiyeseni chonde . . . kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira,” watero Yehova wa makamu.—Mal. 3:10.
Timakonda Yehova “chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Njira ina imene wasonyezera chikondi chimenechi ndi yoti amadalitsa atumiki ake. Tikamakonda kwambiri Mulungu timayambanso kumukhulupirira kwambiri. Timakhulupiriranso kuti iye amapereka mphoto kwa anthu amene amawakonda. (Aheb. 11:6) Yehova ndi Mulungu wopereka mphoto. Sitinganene kuti timakhulupirira Mulungu ngati sitikhulupirira kuti iye amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.” (Aheb. 11:1) Choncho ngati timakhulupirira Mulungu tiyeneranso kukhulupirira kuti amadalitsa atumiki ake. Mulemba la leroli, Yehova akutilonjeza kuti tikakhala okhulupirika kwa iye, azitidalitsa. Tikamachita zimene lembali likunena, timasonyeza kuti timayamikira zimene Yehova watilonjezazi. w16.12 4:1-3
Lachinayi, April 26
Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa.—Aroma 8:6.
Mkhristu amene watumikira kwa nthawi yaitali angayambe kuika maganizo ake pa zinthu za thupi. Koma izi sizikutanthauza kuti n’kulakwa kuganizira nthawi zina za chakudya, ntchito, zosangalatsa komanso kukondana m’banja. Mtumiki wa Yehova aliyense akhoza kuganizira zimenezi. Paja nayenso Yesu ankadya komanso kudyetsa anthu. Iye ankadziwanso kuti kupeza nthawi yosangalala n’kofunika. Ndipo mtumwi Paulo anasonyezanso kufunika kosonyezana chikondi m’banja. Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti kuika maganizo amasonyeza kuti maganizo onse, mapulani onse komanso mtima wonse uli pa chinthu chinachake. Anthu amene amatsatira zofuna za thupi nthawi zonse amangochita zimene thupi lochimwali limalakalaka. Katswiri wina ananena kuti mawu oti “kuika maganizo” omwe ali pa Aroma 8:5 amanena za munthu amene amakonda kwambiri zimene thupi lake limalakalaka. Munthuyo amalankhulalankhula za zinthu zimenezo ndipo amasangalala akamazichita. w16.12 2:5, 9, 10
Lachisanu, April 27
Iwe ndiwe ndani, kuti uziweruza mnzako?—Yak. 4:12.
Tonsefe tingayambe kuchita zinthu modzikuza ngati titalola kuti zilakolako za thupi zizititsogolera. Anthu ambiri amayamba kudzikuza chifukwa cha nsanje, kufuna udindo komanso chifukwa chosaugwira mtima. Anthu ena a m’Baibulo monga Abisalomu, Uziya komanso Nebukadinezara anayamba kudzikuza chifukwa chotsatira “ntchito za thupi” ndipo Yehova anawachititsa manyazi. (2 Sam. 15:1-6; 18:9-17; 2 Mbiri 26:16-21; Dan. 5:18-21) Koma palinso zifukwa zina zimene zingapangitse munthu kuti achite zinthu zooneka ngati si wodzichepetsa. Mwachitsanzo, taganizirani za Abimeleki ndi Petulo. (Gen. 20:2-7; Mat. 26:31-35) Kodi anthu amenewa tingati anali odzikuza? Kapena vuto ndi loti sankadziwa zonse kapena anachita zinthu asanaganize kaye? Popeza sitidziwa zamumtima mwa munthu, si bwino kuthamangira kuweruza ena. w17.01 3:9, 10
Loweruka, April 28
Mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.—Luka 21:4.
Mofanana ndi mayi wamasiyeyu, masiku ano abale ndi alongo ambiri amakhulupirira kuti akamafunafuna Ufumu choyamba, Yehova adzawapatsa zofunika pa moyo. (Mat. 6:33) Chitsanzo ndi m’bale wina dzina lake Malcolm. Kwa zaka zambiri, iye ndi mkazi wake anakhala akutumikira Yehova ndipo anakumana ndi mavuto ambiri. Iye anati: “Nthawi zina zinthu zimasintha mosayembekezereka ndipo zimakhala zovuta kupirira. Koma Yehova amadalitsa anthu amene amamudalira.” M’bale Malcolm anapereka malangizo akuti: “Muzipemphera kuti Yehova akuthandizeni kuchita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Ndipo muziganizira kwambiri zinthu zimene mungathe kuchita osati zomwe simungakwanitse.” Pamene dzikoli ‘likuipiraipirabe’ tizikumana ndi mavuto ambirimbiri. (2 Tim. 3:1, 13) Koma tisamalole kuti mavuto amene tikukumana nawo atifooketse. M’malomwake tizikhulupirira kwambiri Yehova n’kumachita zimene tingathe. w17.01 1:17-19
Lamlungu, April 29
Si iwe amene udzandimangira nyumba.—1 Mbiri 17:4.
Davide anakhumudwa poona kuti panalibe kachisi wa Yehova choncho anaganiza zoti amange kachisiyo. Koma lemba lalero likusonyeza kuti maganizo a Yehova anali osiyana ndi amenewa. Ngakhale kuti Yehova analonjeza kuti adzapitiriza kudalitsa Davide, ananena kuti Solomo ndi amene adzamange kachisi. Ndiye kodi Davide anatani atamva zimenezi? (1 Mbiri 17:1-4, 8, 11, 12; 29:1) Davide akanatha kukhumudwa kwambiri chifukwa choti ankafunitsitsa kumanga kachisi wa Yehova. Koma anathandiza kwambiri pokonzekera ntchito imene Solomo adzagwireyo. Anapeza zitsulo, mkuwa, siliva, golide matabwa komanso anthu oti adzagwire ntchitoyo. Iyeyo sanadandaule kuti akapanda kumanga kachisiyo sadzatamandidwa. Ndipotu atamangidwa ankatchedwa kachisi wa Solomo. M’malomwake analimbikitsa Solomo kuti: “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendere bwino kuti umange nyumba ya Yehova.”—1 Mbiri 22:11, 14-16. w17.01 5:6, 7
Lolemba, April 30
Tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu.—Sal. 79:9.
Ngakhale tikamazunzidwa, tiziyesetsa kutsatira mfundo za Mulungu ndi malamulo ake. Tikamachita zinthu zabwino, timaonetsa kuwala kwathu ndipo dzina la Yehova limalemekezedwa. (Mat. 5:14-16) Tikamakhala oyera, timasonyeza kuti malamulo a Yehova ndi abwino ndipo zonena za Satana ndi zabodza. Koma tikachimwa, tiyenera kulapa mochokera pansi pa mtima ndipo tisamachitenso makhalidwe alionse amene anganyozetse dzina la Yehova. Yehova amagwiritsa ntchito dipo kuti akhululukire anthu amene asonyeza chikhulupiriro. Dipo limapangitsanso kuti azilandira anthu amene adzipereka kwa iye ndipo amawaona kuti ndi olungama. Yehova amaona Akhristu odzozedwa ngati ana ake ndipo a “nkhosa zina” ngati mabwenzi ake. (Yoh. 10:16; Aroma 5:1, 2; Yak. 2:21-25) Choncho, panopa dipo limatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu komanso kuti tiziyeretsa nawo dzina lake. w17.02 2:5, 6