May
Lachiwiri, May 1
Aamoni anagonja.—Ower. 11:33.
Yefita ankadziwa kuti akufunika thandizo la Yehova kuti apulumutse Aisiraeli m’manja mwa Aamoni. Iye analonjeza Yehova kuti: ‘Ndidzapereka aliyense amene adzatuluke m’nyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere kuchokera kwa ana a Amoni. Ndidzam’pereka monga nsembe yopsereza.’ (Ower. 11:30, 31) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Yehova amadana ndi kupha anthu n’cholinga choti aperekedwe nsembe. Choncho Yefita sankafuna kupha aliyense n’kumupereka nsembe. (Deut. 18:9, 10) Aisiraeli analamulidwa kuti azipereka nyama yathunthu ngati nsembe yopsereza. Choncho Yefita ankatanthauza kuti munthu amene adzamuchingamireyo adzatumikira pachihema cha Yehova kwa moyo wake wonse. Yehova anamva pemphero la Yefita ndipo anamuthandiza kugonjetsa adani ake. (Ower. 11:32) Pamene Yefita ankabwera, mwana wake wamkazi ndi amene anamuchingamira. Apa tsopano zinthu zinavuta chifukwa mwana wake anali yekhayo. Ndiye kodi Yefita anatani? Kodi anaperekadi mwana wakeyu kuti akatumikire pachihema moyo wake wonse? w16.04 1:11-13
Lachitatu, May 2
Iwo anapitiriza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuwerenga.—Neh. 8:8.
Zaka za m’mbuyumu mipingo yambiri inaphunzira buku lakuti, Yandikirani kwa Yehova pa Phunziro la Baibulo la Mpingo. M’bukuli tinaphunzira za makhalidwe a Mulungu. Tinalimbikitsidwanso ndi mayankho ochokera pansi pa mtima a abale ndi alongo ndipo izi zinatithandiza kuti tizikonda kwambiri Atate wathu wakumwamba. Tikakhala pamisonkhano n’kumamvetsera nkhani, zitsanzo komanso kuwerenga Baibulo, timamvetsa bwino Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zothandiza zimene mumapeza mukamakonzekera komanso kumvetsera mfundo zazikulu mlungu uliwonse. Misonkhano imatithandizanso kuti tizitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. (1 Ates. 4:9, 10) Chitsanzo ndi mfundo zimene timaphunzira pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Kodi inuyo munaphunzirapo mfundo zina zimene zinakuthandizani kusintha zolinga, kukhululukira Mkhristu mnzanu kapena kuyamba kupemphera kuchokera pansi pa mtima? Misonkhano imene timakhala nayo mkati mwa mlungu imatithandizanso kuti tizilalikira mwaluso komanso kuphunzitsa mfundo za m’Baibulo mogwira mtima.—Mat. 28:19, 20. w16.04 3:4, 5
Lachinayi, May 3
Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.—Aroma 15:4.
Baibulo limafotokoza za anthu ena amene anasemphana maganizo. Mwachitsanzo, machaputala oyambirira a buku la Genesis amanena za Kaini ndi Abele. (Gen. 4:3-8) Nayenso Lameki anapha munthu amene anamumenya. (Gen. 4:23) Komanso abusa a Abulahamu (Abulamu) ndi a Loti anakangana. (Gen. 13:5-7) Hagara ankanyoza Sara (Sarai) ndipo Sarayo anakwiyira Abulahamu. (Gen. 16:3-6) Baibulo linaneneratunso kuti dzanja la Isimaeli lidzalimbana ndi aliyense ndipo dzanja la aliyense lidzalimbana ndi la Isimaeli. (Gen. 16:12) N’chifukwa chiyani nkhani zimenezi zinalembedwa m’Baibulo? Chifukwa china n’chakuti nkhani zoterezi zimatithandiza kumvetsa ubwino woyesetsa kukhala mwamtendere ndi ena. Timapindula kwambiri tikamaphunzira m’Baibulo za anthu amene analimbana ndi mavuto. Timaona zimene anachita komanso mmene zingatithandizire tikakumana ndi mavuto ofanana ndi amene anakumana nawo. Mwachidule tingati timadziwa zoyenera kuchita tikakumana ndi mavuto. w16.05 1:1, 2
Lachisanu, May 4
Komanso, m’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe choyamba.—Maliko 13:10.
Yesu ndi ophunzira ake ankagwiritsa ntchito njira ziti akamalalikira? Iwo ankalalikira kulikonse kumene kunkapezeka anthu, kaya ndi m’misewu kapena m’misika. Ankapitanso kunyumba ndi nyumba n’kumafufuza anthu oyenera. (Mat. 10:11; Luka 8:1; Mac. 5:42; 20:20) Njira imeneyi inkathandiza kuti azilalikira kwa anthu onse. Nanga kodi a Mboni amachita bwanji pa nkhaniyi? Iwo amalalikira kuti Yesu wakhala akulamulira kuyambira mu 1914. Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, iwo amaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Buku lina linati: “A Mboni za Yehova amaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuposa chilichonse. Akaona anthu akuvutika ndi zinthu monga njala komanso matenda amawathandiza. . . . Koma amadziwa kuti ntchito yawo yaikulu ndi kuuza anthu za mapeto a dzikoli komanso zimene angachite kuti adzapulumuke.” (Pillars of Faith—American Congregations and Their Partners) A Mboni za Yehova amalalikira potsatira njira zimene Yesu ndi ophunzira ake ankagwiritsa ntchito. w16.05 2:10, 12
Loweruka, May 5
Udzamvetsa tanthauzo la kuopa Yehova ndipo udzamudziwadi Mulungu.—Miy. 2:5.
Tikamayesetsa kusankha zinthu mogwirizana ndi maganizo a Yehova, ubwenzi wathu ndi iye umalimba. (Yak. 4:8) Komanso iye amasangalala nafe ndiponso amatidalitsa. Zimenezi zimapangitsa kuti tizikhulupirira kwambiri Atate wathu wakumwamba. Choncho tiyeni tiziyesetsa kutsatira malamulo ndi mfundo za m’Baibulo popeza zimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. N’zoona kuti kuphunzira za Yehova sikudzatha. (Yobu 26:14) Komabe tikamachita khama kuphunzira za iye, tingakhale anzeru, odziwa zinthu komanso ozindikira ndipo tingasankhe zochita mwanzeru. (Miy. 2:1-5) Maganizo ndi zochita za anthu zimasintha pakapita nthawi. Koma Baibulo limati: “Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale. Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.” (Sal. 33:11) Izi zikusonyeza kuti tikamasankha zochita mogwirizana ndi maganizo a Yehova, yemwe ndi wanzeru, timasankha mwanzeru. w16.05 3:17
Lamlungu, May 6
Yehova amaona mmene mtima ulili.—1 Sam. 16:7.
Tisamaweruze anthu a m’gawo lathu komanso Akhristu anzathu podziwa kuti Yehova amaona mtima. (Yoh. 6:44) Mfundo yoti Yehova amaona mitima komanso ndi amene amaumba anthu, imatithandiza kuti tiziona Akhristu anzathu moyenera. (Yes. 64:8) Kodi mumaona abale ndi alongo anu ngati mmene Yehova amawaonera, kuti ndi anthu oti akuumbidwabe? Popeza Yehova amaona mtima, amadziwa kuti munthu akhoza kusintha ndipo saganizira kwambiri zimene amalakwitsa. (Sal. 130:3) Tingatsanzire Mulungu ngati ifenso timaona kuti Akhristu anzathu akhoza kusintha. Ndipotu tingathe kuthandiza Mulungu pa ntchito yake youmba anthu tikamathandiza abale ndi alongo kuti akhale olimba mwauzimu. (1 Ates. 5:14, 15) Akulu, omwe ndi “mphatso za amuna,” ayenera kukhala patsogolo pochita zimenezi.—Aef. 4:8, 11-13. w16.06 1:4-6
Lolemba, May 7
Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.—1 Akor. 10:12.
Kugwira nawo ntchito yolalikira kungapangitse kuti tikhale odzichepetsa komanso kuti tikhale ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Kodi inuyo ntchito yolalikira yakuthandizani kukhala ndi makhalidwe ati? Chofunikanso n’chakuti tikakhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, anthu amakopeka ndi uthenga wathu. Chitsanzo ndi zimene zinachitika ku Australia. Pamene a Mboni awiri ankalalikira, anakumana ndi mayi wina amene anawalankhula mwachipongwe. Koma a Mboniwo anamvetsera mwaulemu zonse zimene mayiyo ananena. Patapita nthawi mayiyo anazindikira kuti sanachite bwino, ndipo analemba kalata yopepesa ku ofesi ya nthambi. M’kalatayo anati: “Mundipepesere kwa anthuwa chifukwa ngakhale kuti ndinalankhula zachipongwe, iwo anali oleza mtima komanso odzichepetsa. Ndikuona kuti ndinachita zopusa ponyoza anthu amene ankalalikira Mawu a Mulungu.” Kodi mayiyu akanalemba zimenezi zikanakhala kuti a Mboniwo anapsa mtima n’kumubwezera chipongwe? Izitu zikusonyeza kuti ntchito yolalikira imathandiza ifeyo komanso anthu amene timawalalikira. w16.06 2:12, 13
Lachiwiri, May 8
Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.—Mat. 22:39.
Anthufe tinatengera uchimo wa Adamu choncho si ife angwiro. (Aroma 5:12, 19) Izi zingachititse kuti anthu ena alankhule kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa. Kupanda kusamala, zoterezi zingachititse kuti tisiye kukonda Yehova ndi anthu ake. Kodi inuyo mungatani wina atakukhumudwitsani? Mwachitsanzo, Eli, yemwe anali Mkulu wa Ansembe, anali ndi ana awiri amene sankatsatira malamulo a Yehova. Baibulo limati: “Ana aamuna a Eli anali anthu opanda pake. Iwo anali kunyalanyaza Yehova.” (1 Sam. 2:12) Ngakhale kuti bambo awo ankalimbikitsa kulambira koona, anawa ankachita machimo akuluakulu. Eli ankadziwa zimene anawa ankachita koma sankawadzudzula mwamphamvu. Izi zinachititsa kuti Mulungu alange banja lonse la Eli ndipo anthu a m’banja lake anasiya kukhala akulu a ansembe. (1 Sam. 3:10-14) Kodi inuyo mukanatani mukanakhalapo pa nthawi imene Eli ankalekerera ana akewa? Kodi mukanakhumudwa mpaka kufika posiya kutumikira Mulungu? w16.06 4:5, 6
Lachitatu, May 9
Zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.—Mat. 6:33.
N’chifukwa chiyani Yesu ananena mawu apamwambawa? Iye anali atafotokoza chifukwa chake pamene anati: “Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.” Ponena kuti “zinthu zonsezi” ankatanthauza zofunika pa moyo. Yehova amatha kudziwiratu zimene munthu akufunikira pa nkhani ya chakudya, zovala komanso pogona, mwinanso munthuyo asanadziwe n’komwe. (Afil. 4:19) Mwachitsanzo, amadziwa kuti ndi chovala chanu chiti chimene chidzayambe kutha. Amadziwanso chakudya choyenera kwa inu komanso malo amene angakhale oyenera kwa inu mogwirizana ndi kukula kwa banja lanu. Ndipotu amaonetsetsa kuti tili ndi zofunika pa moyo. Tisamakayike kuti tikamaika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba, Yehova adzonetsetsa kuti tikupeza zofunika pamoyo. “Mtima wodzipereka kwa Mulungu” ungatithandize kuti tizikhutira ndi “chakudya, zovala ndi pogona.”—1 Tim. 6:6-8. w16.07 1:17, 18
Lachinayi, May 10
Pamene tinali adani, tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake.—Aroma 5:10.
Tikayanjanitsidwa ndi Mulungu timakhala naye pa mtendere. Paulo anasonyezanso kuti izi zimatheka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehovayo. Ponena za iyeyo ndi odzozedwa anzake, analemba kuti: “Chotero, popeza tsopano tayesedwa olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro, tiyeni tikhale pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Mwa ameneyunso, ndiponso chifukwa cha chikhulupiriro, takhala ndi ufulu wolowa m’kukoma mtima kwakukulu, mmene tilimo tsopano.” (Aroma 5:1, 2) Kunena zoona awatu ndi madalitso osaneneka. Mwachibadwa anthufe ndife osalungama. Koma mneneri Danieli ananeneratu kuti m’masiku otsiriza ‘anthu ozindikira [odzozedwa amene ali padzikoli] adzathandiza anthu ambiri kukhala olungama.’ (Dan. 12:3) Ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa yathandiza a “nkhosa zina” ambirimbiri kukhala olungama pamaso pa Yehova. (Yoh. 10:16) Zonsezi zikuchitika chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.—Aroma 3:23, 24. w16.07 3:10, 11
Lachisanu, May 11
Anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.—Gen. 6:2.
Angelowa ndi akaziwo anabereka ziphona zankhanza zotchedwa Anefili. Komanso ‘kuipa kwa anthu kunachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha.’ (Gen. 6:1-5) Yehova anabweretsa Chigumula m’nthawi ya Nowa ndipo chinawononga anthu onse oipa. Pa nthawiyo anthu ankangotanganidwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku monga kukwatira ndi kukwatiwa. Iwo sankamvetsera uthenga woti Mulungu awononga dziko umene Nowa, yemwe anali “mlaliki wa chilungamo,” ankalalikira. (2 Pet. 2:5) Yesu ananeneratu kuti zimene zinkachitikazo zidzachitikanso masiku otsiriza ano. (Mat. 24:37-39) Masiku ano anthu ambiri samvetsera uthenga wa Ufumu. Uthengawu ukulalikidwa padziko lonse kuti ukhale umboni ku mitundu yonse ndipo kenako mapeto afika. Koma ifeyo tisalole kuti zinthu ngati banja komanso kulera ana zitilepheretse kukhala maso podziwa kuti tsiku la Yehova lili pafupi. w16.08 1:8, 9
Loweruka, May 12
Nthawi yotsalayi yafupika. Choncho amene ali ndi akazi azikhala ngati alibe . . . amene amagwiritsira ntchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwiritsira ntchito mokwanira.—1 Akor. 7:29-31.
Popeza tili kumapeto kwenikweni kwa “masiku otsiriza,” tikukhala m’nthawi “yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1-5) Koma kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kungathandize kuti dzikoli lisatisokoneze. Polemba mawu amulemba la leroli, Paulo sankauza anthu apabanja kuti azinyalanyaza udindo wawo. Koma ankangowakumbutsa kuti aziika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba chifukwa nthawi yotsalayi yafupika. (Mat. 6:33) Monga tanena kale, tikukhala m’masiku ovuta ndipo mabanja ambiri akusokonekera. Koma n’zotheka kukhala ndi banja losangalala. Akhristu akamayesetsa kukhalabe m’gulu la Yehova, kutsatira malangizo a m’Malemba komanso kulola kuti mzimu wa Yehova uziwatsogolera, banja lawo limayenda bwino. Izi zimathandiza kuti asalekanitse “chimene Mulungu wachimanga pamodzi.”—Maliko 10:9. w16.08 2:17, 18
Lamlungu, May 13
Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.—1 Pet. 5:2.
M’gulu la Yehova mukufunika abale ambiri oti akhale abusa. Anthu amene adzakhale pa udindowu amafunika kuphunzitsidwa. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambiri zokhudza ine, zimenezo uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:1, 2) Timoteyo anaphunzira zambiri chifukwa ankayenda ndi Paulo yemwe anali wachikulire. Kenako nayenso ankagwiritsa ntchito njira zimene anaphunzirazo akamalalikira komanso pochita zinthu zina. (2 Tim. 3:10-12) Sikuti Paulo ankangomusiya Timoteyo kuti aziphunzira yekha zinthu. M’malomwake ankayenda naye n’kumamuphunzitsa. (Mac. 16:1-5) Akulu angatsanzire Paulo pomatenga atumiki othandiza popita ku maulendo aubusa ngati akuona kuti n’zoyenera kutero. Akamachita zimenezi amawathandiza kuti akadzakhala oyang’anira azidzaphunzitsa bwino. Atumikiwo amaphunziranso makhalidwe monga chikhulupiriro, kuleza mtima komanso chikondi. Izi zidzawathandizanso kuti adzakhale abusa abwino a “gulu la nkhosa za Mulungu.” w16.08 4:16, 17
Lolemba, May 14
Usalefuke.—Zef. 3:16.
Nthawi zina, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti manja a lende potanthauza munthu amene wafooka, wataya mtima kapena akuganiza kuti zinthu sizidzakhalanso bwino. (2 Mbiri 15:7; Aheb. 12:12) Munthu wotereyu sachedwa kukhumudwa kapena kugwa ulesi. M’dziko la Satanali, timapanikizika ndi zinthu zambiri ndipo timakhala ndi nkhawa. Timakhala ngati boti limene amangirirapo nangula moti silingayendenso. (Miy. 12:25) Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zimatichititsa kukhala ndi nkhawa? Ndi zinthu monga imfa ya mnzathu kapena m’bale wathu, matenda, mavuto azachuma komanso kutsutsidwa. Zinthu zoterezi zingachititsenso kuti tizingokhala okhumudwa komanso tilefuke. Komabe tisamaiwale kuti Mulungu ndi wokonzeka kutithandiza.—Yes. 41:10, 13. w16.09 1:2, 4
Lachiwiri, May 15
Ndidzamvera malamulo anu, Chifukwa mwandichititsa kuwamvetsa bwino.—Sal. 119:32.
Akhristu ambiri akuyesetsa kuti athane ndi zinthu zimene amalakwitsa. Ena akuyesetsa kuti azikondabe ntchito yolalikira. Ndiye palinso ena amene akuvutika chifukwa cha matenda kapena kusowa wocheza naye. Enanso zikuwavuta kukhululukira munthu amene anawakhumudwitsa kapena kuwalakwira. Kaya tinabatizidwa liti, tonsefe tiyenera kulimbana ndi zimene zingatilepheretse kutumikira bwino Yehova. Tisamaiwale kuti iye amadalitsa anthu okhulupirika. Ngati mwazindikira kuti pali mbali ina imene simukuchita bwino, pemphani Yehova kuti akupatseni mzimu woyera. Pemphero ndiponso mzimu woyera zingakuthandizeni kuti muchite zoyenera komanso kuti Yehova akudalitseni. Muyeneranso kuchita mogwirizana ndi mapemphero anu. Muziwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso muzipeza nthawi yophunzira panokha ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja.—Sal. 119:32. w16.09 2:10, 11
Lachitatu, May 16
Chikhulupiriro ndicho . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.—Aheb. 11:1.
Mwina anthu ena anakuuzanipo kuti: “Ndimakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina chifukwa choti asayansi amanena choncho. N’chifukwa chiyani inu mumakhulupirira kuti kuli Mulungu ngati munamuonapo?” N’zoona kuti palibe munthu amene anaonapo Mulungu kapena kuona zinthu zikulengedwa. (Yoh. 1:18) Koma anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina, nawonso amakhulupirira zinthu zoti sanazionepo. Palibe munthu amene anaona chamoyo chikusintha n’kukhala chinthu china. Mwachitsanzo, palibe anaonapo buluzi akusintha n’kukhala mkango. (Yobu 38:1, 4) Choncho kaya munthu amakhulupirira zotani, ayenera kufufuza mokwanira komanso kugwiritsa ntchito luso lakuganiza kuti apeze umboni wa zimene amakhulupirirazo. Ponena za chilengedwe, mtumwi Paulo anati: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.”—Aroma 1:20. w16.09 4:4
Lachinayi, May 17
Musaiwale kuchereza alendo.—Aheb. 13:2.
Yehova anapereka malamulo othandiza anthu amene anasamukira ku Isiraeli. Limodzi mwa malamulowo linali lowalola kuti azikunkha zotsala m’minda. (Lev. 19:9, 10) M’malo mongouza Aisiraeli kuti azilemekeza anthu a mitundu ina, Yehova anawauza kuti aziganizira mmene anthuwo akumvera. (Eks. 23:9) Aisiraeli ankadziwa ‘mmene zimakhalira munthu akakhala mlendo.’ Ngakhale pamene sanali akapolo, Aiguputo ankawasalabe chifukwa chosiyana mitundu ndi chipembedzo. (Gen. 43:32; 46:34; Eks. 1:11-14) Aisiraeli anavutika kwambiri pamene anali alendo komabe Yehova ankafuna kuti iwo aziona anthu a mitundu ina okhala pakati pawo “ngati mbadwa” za m’dzikolo. (Lev. 19:33, 34) Masiku anonso Yehova amaganizira anthu a mitundu ina amene timasonkhana nawo. (Deut. 10:17-19; Mal. 3:5, 6) Tikamaganizira mavuto amene akukumana nawo, monga kusalidwa komanso kusadziwa chinenero, tingapeze njira zowathandizira.—1 Pet. 3:8. w16.10 1:3-5
Lachisanu, May 18
Monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa, nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.—Yak. 2:26.
Yakobo analemba zokhudza chikhulupiriro m’kalata yake ndipo anafotokoza kuti munthu wachikhulupiriro chenicheni amachita ntchito zosonyeza chikhulupiriro chakecho. Iye analemba kuti: “Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.” (Yak. 2:18) Yakobo anafotokozanso kuti kungokhulupirira n’kosiyana ndi kuchita ntchito zosonyeza chikhulupiriro. Mwachitsanzo, ziwanda zimakhulupirira kuti kuli Mulungu, koma sitinganene kuti zili ndi chikhulupiriro chenicheni. Tikutero chifukwa zimachita zinthu zotsutsana ndi Mulungu. (Yak. 2:19, 20) Koma Abulahamu anali ndi chikhulupiriro chenicheni. Ponena za iye, Yakobo anati: “Kodi Abulahamu atate wathu sanayesedwe wolungama chifukwa cha ntchito zake, atapereka Isaki mwana wake nsembe paguwa? Waonatu kuti chikhulupiriro chake chinayendera limodzi ndi ntchito zake, ndipo mwa ntchito zakezo chikhulupiriro chakecho chinakhala changwiro.” (Yak. 2:21-23) Ndiyeno potsindika mfundo yoti chikhulupiriro chiyenera kusonyezedwa ndi ntchito, Yakobo analemba mawu amulemba la lerowa. w16.10 4:8
Loweruka, May 19
Anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.—Mlal. 3:11.
Asayansi agwiritsa ntchito zinthu zimene adziwa zamlengalenga komanso zapadzikoli popanga zinthu zomwe zathandiza anthu. Komabe iwo sanathe kupeza mayankho a mafunso ambiri. Mwachitsanzo, sangatiuze kuti chilengedwe chinakhalapo bwanji komanso kuti n’chifukwa chiyani anthufe ndiponso zinthu zina zamoyo zili padzikoli. Komanso anthu sangafotokoze chomwe chimachititsa kuti tizifuna kukhala ndi moyo wosatha. N’chifukwa chiyani amalephera kuyankha mafunso ngati amenewa? Chifukwa china n’choti asayansi ndi anthu ena amati kulibe Mulungu ndipo amalimbikitsa mfundo yoti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina. Koma Baibulo limapereka mayankho ogwira mtima a mafunso ofunikawa. Yehova anaika malamulo osiyanasiyana m’chilengedwe ndipo malamulowo sasintha. Anthu ogwira ntchito zamagetsi, mapulambala, mainjiniya, oyendetsa ndege komanso ochita opaleshoni amadalira malamulo a m’chilengedwewa. w16.11 2:4, 5
Lamlungu, May 20
Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.—Mac. 17:28.
Pali zinthu zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova. Iye ndi amene anatipatsa moyo ndipo pakanapanda iye si bwenzi tiliko. Watipatsanso Baibulo, lomwe ndi mphatso yapadera kwambiri. Mofanana ndi Akhristu a ku Tesalonika, timaona kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri chifukwa muli uthenga wochokera kwa Mulungu. (1 Ates. 2:13) Baibulo latithandiza kuti tiyandikire Mulungu komanso kuti iye atiyandikire. (Yak. 4:8) Atate wathu wakumwamba watipatsa mwayi wokhala m’gulu lake. Tiyenera kuyamikira kwambiri mwayi umenewu. Wamasalimo anasonyeza kuyamikira pamene anaimba kuti: “Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino: Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” (Sal. 136:1) Mu Salimo 136, timapeza mawu akuti “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale” maulendo 26. Tikakhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake, tidzaona kukwaniritsidwa kwa mawuwa chifukwa tidzakhala ndi moyo wosatha. w16.11 3:18, 19
Lolemba, May 21
Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.—Aroma 5:12.
Lembali limapezeka kambirimbiri m’buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? Mukamaphunzira bukuli ndi mwana wanu kapena anthu ena, muyenera kuti mumawerenga lembali mukamakambirana mutu 3, 5 ndi 6. Mituyi imanena za cholinga cha Mulungu kwa anthu, dipo komanso zimene zimachitika munthu akamwalira. Komatu lembali lingatithandizenso tonsefe kuti tiziyamikira ubwenzi wathu ndi Yehova, tiziona zimene tingachite kuti tizimusangalatsa komanso tiziyembekezera zimene walonjeza. N’zoona kuti tonsefe ndife ochimwa ndipo tsiku lililonse timalakwitsa zinthu zina. Koma Mulungu amatichitira chifundo chifukwa amakumbukira kuti ndife fumbi. (Sal. 103:13, 14) M’pemphero la chitsanzo, Yesu ananena kuti tizipempha kuti: “Mutikhululukire machimo athu.” (Luka 11:2-4) Choncho tisamangoganizirabe zinthu zimene Mulungu anatikhululukira. Koma tiziganizira mfundo yoti anatikhululukira ndiponso chifukwa chake anatha kuchita zimenezi. w16.12 1:1-3
Lachiwiri, May 22
Otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi.—Aroma 8:5.
Akhristu a ku Roma anafunika kuonanso zimene ankakonda. Izi zikanawathandiza kudziwa ngati maganizo awo onse anali pa “zinthu za thupi.” Nafenso masiku ano tiyenera kudzifufuza. Kodi timakonda kwambiri chiyani nanga timalankhulalankhula za chiyani? Kodi tsiku lililonse timakonda kuganizira kapena kuchita chiyani? Ena akhoza kuzindikira kuti amangokhalira kulawa mitundu yosiyanasiyana ya vinyo, kukongoletsa nyumba yawo, kufufuza masitayilo a zovala, kusunga ndalama, kupita kokasangalala ndi zina. N’zoona kuti zinthu zimenezi pazokha si zolakwika. Mwachitsanzo, Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo ndipo Paulo anauza Timoteyo kuti azimwa “vinyo pang’ono.” (1 Tim. 5:23; Yoh. 2:3-11) Koma kodi Yesu ndi Paulo ankaona kuti chofunika kwambiri pa moyo wawo ndi vinyo? Kodi iwo ankakonda kwambiri chiyani, nanga ankakonda kulankhula za chiyani? Nanga ifeyo timaona kuti chofunika kwambiri pa moyo wathu n’chiyani? w16.12 2:5, 10, 11
Lachitatu, May 23
Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.—Heb. 13:5.
Lonjezoli limagwirizananso ndi zimene Yesu ananena zoti tikafuna Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu, tidzadalitsidwa. (Mat. 6:33) Pa nthawi ina, Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?” (Mat. 19:27) Yesu sanadzudzule Petulo chifukwa cha funsoli. M’malomwake anauza ophunzira ake kuti adzadalitsidwa chifukwa chololera kusiya zinthu zina. Iye ananena kuti atumwi okhulupirikawo limodzi ndi anthu ena adzalamulira ndi Yesu kumwamba. Koma palinso madalitso ena amene tingapeze panopa. Yesu anati: “Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.” (Mat. 19:29) Apa analonjeza kuti tidzapeza madalitso ambiri. Ndipo n’zoona kuti kupeza abambo, amayi, azichimwene, azichemwali komanso ana m’gulu la Yehova ndi madalitso oposa zimene tinasiya chifukwa cha Ufumu. w16.12 4:4, 5
Lachinayi, May 24
Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.—Aheb. 11:1.
Tikuyembekezera zinthu zofunika komanso zabwino kwabasi. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tikuyembekezera nthawi imene cholinga cha Mulungu choyambirira chidzakwaniritsidwe, dzina lake n’kuyeretsedwa. (Yoh. 10:16; Mat. 6:9, 10) Yehova watilonjezanso moyo wosatha moti Akhristu ena adzapita kumwamba pomwe ena adzakhala padzikoli. (2 Pet. 3:13) Panopa, tikudziwa kuti Yehova apitiriza kutitsogolera komanso kutithandiza m’masiku otsirizawa. Anthu a m’dzikoli amayembekezeranso zinthu zosiyanasiyana koma sakhala otsimikiza ngati zingachitikedi. Mwachitsanzo, amene amatchova juga amayembekezera kuti awina koma sangatsimikize zoti awinadi. Koma Akhristufe timatsimikizira ndi mtima wonse kuti zimene tikuyembekezera zidzachitikadi. w16.10 3:1, 2
Lachisanu, May 25
Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana.—1 Pet. 4:10.
Yehova ndi wokoma mtima ndipo anatipatsa mphatso zosiyanasiyana, luso komanso zinthu zina zimene tingagwiritse ntchito pomutumikira komanso pothandiza ena. (Aroma 12:4-8) Yehova amaona kuti tonsefe tili ngati oyang’anira ndipo izi zimasonyeza kuti amatilemekeza, kutidalira komanso amayembekezera kuti tikwaniritse udindo wathu. Koma zimene tikuchita m’gulu la Yehova zikhoza kusintha nthawi iliyonse. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Poyamba anali awiriwiri ndi Yehova m’chilengedwe chonse. (Miy. 8:22) Kenako anathandiza nawo polenga angelo, zinthu zakumwamba ndi zapadziko lapansi komanso anthu. (Akol. 1:16) Patapita nthawi, anasinthanso n’kubwera padzikoli. Poyamba anali kamwana ndipo kenako anakhala munthu wamkulu. (Afil. 2:7) Iye atafa anaukitsidwa n’kubwerera kumwamba ndipo mu 1914 anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Aheb. 2:9) Pambuyo pa ulamuliro wake wa zaka 1,000, adzapereka Ufumu kwa Yehova kuti “Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28. w17.01 3:11, 12
Loweruka, May 26
Sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira.—Yos. 24:15.
Mayi wina ankafunika kusankha zochita pa nkhani inayake. Ndiye anauza mnzake kuti: “Ingondiuza zoti ndichite osati zoti ndiganizire.” Mayiyu ankafuna kuti angouzidwa zochita m’malo mogwiritsa ntchito mphatso yapadera imene Yehova anatipatsa. Kodi inuyo mumatani ngati mukufunika kusankha zochita? Kodi mumasankha nokha kapena mumafuna kuti ena akusankhireni? Nanga kodi mumayamikira mphatso ya ufulu wosankha imene Yehova anatipatsa? Anthu amasiyana maganizo pa nkhani ya ufulu wosankhayi. Ena amaona kuti anthufe tilibe ufulu wosankha chifukwa Yehova analemberatu zonse zimene zidzachitike pa moyo wathu. Pamene ena amati munthu angakhale ndi ufulu wosankha pokhapokha zitakhala kuti angathe kuchita chilichonse chimene akufuna. Koma Mawu a Mulungu angatithandize kudziwa zoona pa nkhaniyi. Baibulo limanena kuti Yehova anatipatsa ufulu wosankha zochita. w17.01 2:1, 2
Lamlungu, May 27
Mwana wanga Solomo ndi wamng’ono komanso wosakhwima, . . . Ndiyetu ndim’konzere zipangizo zoti adzagwiritsire ntchito.—1 Mbiri 22:5.
Davide akanatha kuganiza kuti Solomo wachepa nayo ntchitoyo. Pajatu kachisiyo anafunika kukhala ‘wokongola ndiponso waulemerero wosaneneka.’ Kuwonjezera pamenepo, Solomo anali adakali “wamng’ono komanso wosakhwima.” Koma Davide ankadziwa kuti Yehova adzathandiza Solomo kuti agwire bwino ntchitoyo. Choncho Davide anangochita zimene akanatha ndipo anamuthandiza kukonzekera ntchito yaikuluyo. Nawonso abale achikulire asamakhumudwe pakafunika kuti apatse abale achinyamata ntchito imene iwo ankagwira. Ayenera kudziwa kuti achinyamata akaphunzitsidwa bwino n’kutenga udindo zimathandiza kuti ntchito iziyenda bwino. Abale achikulire ayenera kusangalala akaona kuti achinyamata amene anawaphunzitsa akuyenerera udindo. w17.01 5:8, 9
Lolemba, May 28
Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako.—Gen. 3:15.
Yesu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzaphwanya mutu wa njoka ndipo adzachotseratu mavuto onse obwera chifukwa cha zochita za Satana. Yesu ali padzikoli anathandiza ophunzira ake kuzindikira kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri. Atangobatizidwa anayamba kulalikira “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu” m’madera osiyanasiyana. (Luka 4:43) Iye atatsala pang’ono kupita kumwamba, anauza ophunzira ake kuti adzakhala mboni zake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:6-8) Ntchito yolalikira ikuthandiza anthu padziko lonse kuti adziwe za dipo komanso kuti akhale nzika za Ufumu wa Mulungu. Tikamathandiza abale a Khristu pa ntchitoyi timasonyeza kuti tili kumbali ya Ufumuwo.—Mat. 24:14; 25:40. w17.02 2:7, 8
Lachiwiri, May 29
[Khristu] anapereka ena monga atumwi.—Aef. 4:11.
Ngakhale kuti bungwe lolamulira ndi limene linkatsogolera mpingo woyambirira, iwo ankadziwa kuti Mtsogoleri wawo ndi Yesu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khristu.” (Aef. 4:15) Choncho m’malo modziwika ndi mayina a atumwi, “ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.” (Mac. 11:26) N’zoona kuti Paulo ankadziwa kufunika ‘kosunga miyambo,’ kapena kuti kutsatira mfundo zogwirizana ndi Malemba zimene atumwi ndi akulu ena ankapereka. Koma iye ananenanso kuti: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense [kuphatikizapo aliyense wa m’bungwe lolamulira] ndi Khristu . . . ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:2, 3) Apa zikuoneka kuti Yesu Khristu ndi amene ankatsogolera mpingo mogonjera Mutu wake, Yehova Mulungu. w17.02 4:7
Lachitatu, May 30
Akulu otsogolera bwino apatsidwe ulemu waukulu.—1 Tim. 5:17.
Kupereka ulemu kwa anthu oyenera kulemekezedwa kumatithandizanso ifeyo. Kumatithandiza kuti tisamadzikweze anthu ena akatilemekeza. Komanso kumatithandiza kuti tizigwirizana ndi gulu la Yehova limene limatilangiza kuti tisamalemekeze anthu monyanyira, kaya ndi a Mboni anzathu kapena ayi. Kupereka ulemu woyenera kumathandizanso kuti tisadzakhumudwe kwambiri munthu amene timam’patsa ulemuyo akadzachita zolakwika. Chofunika kwambiri n’chakuti tikamapereka ulemu woyenera, timalemekeza Mulungu. Timakhala kuti tikuchita zimene iye amafuna komanso timasonyeza kuti ndife okhulupirika. Zimenezi zimathandiza kuti ayankhe Satana, amene amamutonza. (Miy. 27:11) Ambiri m’dzikoli amapereka ulemu wonyanyira kwa anthu. Koma ifeyo tikuthokoza Yehova chifukwa amatiphunzitsa zoyenera kuchita pa nkhaniyi. w17.03 1:13, 20, 21
Lachinayi, May 31
[Yehosafati] anachita zoyenera pamaso pa Yehova.—2 Mbiri 20:32.
Mofanana ndi bambo ake, Asa, Yehosafati analimbikitsa anthu kuti afunefune Yehova. Anayambitsa ntchito yapadera yophunzitsa anthu “pogwiritsira ntchito buku la chilamulo cha Yehova.” (2 Mbiri 17:7-10) Yehosafati anafika mpaka kudera la Efuraimu lomwe linali mu ufumu wa kumpoto wa Isiraeli ndipo anathandiza anthu kuti abwerere kwa Yehova. (2 Mbiri 19:4) Ifenso tikhoza kuthandiza kwambiri pa ntchito yophunzitsa anthu imene Yehova akufuna kuti izigwiridwa masiku ano. Kodi inuyo mumafunitsitsa kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu mwezi uliwonse n’cholinga choti ayambe kutumikira Yehova? Ngati titachita khama, Yehova angatithandize kuti tiyambe kuphunzira Baibulo ndi munthu. Kodi mumapempha Yehova kuti akuthandizeni pa nkhaniyi? Nanga mumayesetsa kuphunzira ndi anthu ngakhale pa nthawi imene mukanafuna kupuma? Paja Yehosafati anakathandiza anthu a ku Efuraimu kuti abwerere kwa Yehova. Nafenso tingachite bwino kuthandiza anthu amene anafooka kuti ayambirenso kutumikira Mulungu. w17.03 3:10, 11