Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es18 tsamba 57-67
  • June

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • June
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2018
  • Timitu
  • Lachisanu, June 1
  • Loweruka, June 2
  • Lamlungu, June 3
  • Lolemba, June 4
  • Lachiwiri, June 5
  • Lachitatu, June 6
  • Lachinayi, June 7
  • Lachisanu, June 8
  • Loweruka, June 9
  • Lamlungu, June 10
  • Lolemba, June 11
  • Lachiwiri, June 12
  • Lachitatu, June 13
  • Lachinayi, June 14
  • Lachisanu, June 15
  • Loweruka, June 16
  • Lamlungu, June 17
  • Lolemba, June 18
  • Lachiwiri, June 19
  • Lachitatu, June 20
  • Lachinayi, June 21
  • Lachisanu, June 22
  • Loweruka, June 23
  • Lamlungu, June 24
  • Lolemba, June 25
  • Lachiwiri, June 26
  • Lachitatu, June 27
  • Lachinayi, June 28
  • Lachisanu, June 29
  • Loweruka, June 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2018
es18 tsamba 57-67

June

Lachisanu, June 1

Ndidzam’pereka monga nsembe yopsereza.​—Ower. 11:31.

Paja Yefita analibe mwana wina. Choncho ankayembekezera kuti mwana wakeyu ndi amene adzatenge dzina lake komanso kulandira cholowa cha banja lawo. (Ower. 11:34) Ngakhale zinali choncho, Yefita ananena kuti: “Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.” (Ower. 11:35) Yehova anasangalala kwambiri ndi zimene Yefita anachita ndipo anamudalitsa. Kodi nanunso mungathe kuchita zimene Yefita anachitazi? Pamene tinkadzipereka kwa Yehova tinamulonjeza kuti tizichita zonse zimene akufuna. Tinkadziwa kuti tiyenera kudzimana zinthu zina kuti tikwanitse kuchita zimenezi. Ngakhale zili choncho, nthawi zina zimakhala zovuta ngati tapemphedwa kuchita zinthu zimene sitinkaganiza kuti tingachite. Komabe tikamalolera timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Ndipotu zotsatira zake zimakhala zabwino chifukwa Yehova amatidalitsa.​—Mal. 3:10. w16.04 1:11, 14, 15

Loweruka, June 2

Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.—Chiv. 2:7.

Yesu amagwiritsa ntchito mzimu woyera potsogolera mpingo. Akhristufe timafunika mzimuwu kuti uzitithandiza kupewa mayesero, kulalikira molimba mtima ndiponso kusankha zinthu mwanzeru. Choncho tiyeni tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano kuti tilandire mzimuwu. Pamisonkhano timaphunziranso zokhudza kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo. Izi zimatithandiza kuti tisamakayikire zimene Mulungu walonjeza. Anthu amene amatilimbikitsa si okamba nkhani okha. Timalimbikitsidwanso kumva abale ndi alongo akuyankha komanso kuimba mochokera pansi pa mtima. (1 Akor. 14:26) Tikamachezanso ndi abale ndi alongo misonkhano isanayambe komanso ikatha, timaona kuti sitili tokha ndipo timasangalala.​—1 Akor. 16:17, 18. w16.04 3:6, 7

Lamlungu, June 3

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.​—Mat. 28:19.

Yesu ananena kuti uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Iye ananenanso kuti tiyenera kuthandiza “anthu a mitundu yonse” kuti akhale ophunzira ake. Zimenezi zikutanthauza kuti ntchito yolalikirayi iyenera kugwiridwa padziko lonse lapansi. Tiyeni tikambirane mfundo zotsimikizira kuti a Mboni za Yehova akukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse. Ku United States kuli atsogoleri pafupifupi 600,000 a zipembedzo zosiyanasiyana. Koma kuli a Mboni za Yehova pafupifupi 1,200,000. Komanso padziko lonse pali ansembe achikatolika ongopitirira pang’ono 400,000. Ndiye taganizirani chiwerengero cha a Mboni amene akulalikira za Ufumu wa Mulungu. Padziko lonse, pali a Mboni oposa 8 miliyoni ndipo akulalikira m’mayiko 240. Apa zikuonekeratu kuti a Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino padziko lonse ndipo ntchito yawo ikuthandiza kuti Yehova atamandike.​—Sal. 34:1; 51:15. w16.05 2:13, 14

Lolemba, June 4

Munthu wokonda kukwiya amayambitsa mkangano, ndipo aliyense wokonda kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.​—Miy. 29:22.

Dziko lapansi ladzaza ndi anthu onyada, odzikuza komanso okonda mpikisano. Anthu oterewa akutsogoleredwa ndi Satana yemwe amafuna kuti tizichita zinthu popanda kuganizira mmene zinthuzo zingakhudzire anthu ena. (Gen. 3:1-5) Zimenezi zimachititsa kuti anthu azidana komanso azikangana. Koma Yesu anaphunzitsa kuti tiziyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu ena zivute zitani. Pa ulaliki wapaphiri, iye anapereka malangizo abwino amene angatithandize kuti tizipewa kukangana. Mwachitsanzo, anauza ophunzira ake kuti ayenera kukhala ofatsa komanso okonda mtendere. Anawauzanso kuti azipewa kupsa mtima, azithetsa mwamsanga kusamvana komanso azikonda adani awo.​—Mat. 5:5, 9, 22, 25, 44. w16.05 1:4, 5

Lachiwiri, June 5

Ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.—Aroma 7:18.

Ambirife tisanabatizidwe tinasinthanso zinthu zambiri kuti moyo wathu uzigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Komabe n’kutheka kuti pali zinthu zina zing’onozing’ono zomwe tiyenera kusintha kuti tizitha kutsanzira kwambiri Mulungu komanso Yesu. (Aef. 5:1, 2; 1 Pet. 2:21) Mwachitsanzo, mwina ndife ovuta, timaopa anthu komanso mwina timakonda kuchita miseche. Kodi mukuona kuti zikukuvutani kwambiri kusintha makhalidwe ngati amenewa? Tiyenera kukumbukira kuti si ife anthu angwiro. (Akol. 3:9, 10) Choncho nthawi ndi nthawi tikhoza kumalakalaka zinthu zoipa kapena kuvutika kudziletsa khalidwe linalake. Ndipo tingapitirizebe kulimbana ndi mavuto ngati amenewa kwa zaka zambiri.​—Yak. 3:2. w16.05 4:3-5

Lachitatu, June 6

Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamulandira monga mwana wake.​—Aheb. 12:6.

Mwina munamvapo munthu akunena kuti: ‘Makolo anga akamandipatsa chilango ndinkangoona ngati akundilakwira. Koma nditakhala ndi ana, ndinayamba kuona kuti makolowo ankachita bwino.’ Tikakula ndi pamene timayamba kuona chilango mmene Yehova amachionera. Timaona kuti n’chothandiza komanso ndi umboni woti makolo athu amatikonda. (Aheb. 12:5, 11) Yehova ndi Atate wathu ndipo amatiumba chifukwa choti amatikonda. Amafuna kuti tikhale anzeru, tizisangalala komanso tizimukonda. (Miy. 23:15) Iye sasangalala tikamavutika komanso safuna kuti tidzafe monga “ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu,” chifukwa cha uchimo wochokera kwa Adamu. (Aef. 2:2, 3) Monga “ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu,” mwina poyamba tinali ndi makhalidwe osamusangalatsa. Ena anali ndi makhalidwe ngati a nyama zakutchire. Koma timayamikira kwambiri kuti Yehova akutiumba ndipo tsopano tili ngati ana a nkhosa.​—Yes. 11:6-8; Akol. 3:9, 10. w16.06 1:7, 8

Lachinayi, June 7

Chotero, aliyense amene adzadzichepetsa ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba.​—Mat. 18:4.

Ana ambiri amakhala odzichepetsa ndipo amafuna kuphunzira zinthu. (Mat. 18:1-3) Choncho makolo anzeru amayesetsa kuphunzitsa ana awo kuti adziwe Mulungu komanso kuti azimukonda. (2 Tim. 3:14, 15) Koma kuti zimenezi zitheke, ayenera kuyamba iwowo kuphunzira Mawu Mulungu, kuwasunga mumtima mwawo ndiponso kuwatsatira. Paja ana amaphunzira mosavuta akamaona zimene makolo awo amachita. Komanso anawo amaona kuti makolo awo akamawalangiza ndi umboni woti iwowo ndiponso Yehova amawakonda. Ifenso tiyenera kumvera Yehova modzichepetsa. Tikatero iye azitiona kuti ndife okondedwa kwambiri ngati mmene ankaonera Danieli. (Dan. 10:11, 19) Komanso adzapitiriza kutiumba pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake komanso gulu lake. w16.06 2:14, 17

Lachisanu, June 8

Ndapeza Davide mwana wa Jese, munthu wapamtima panga.—Mac. 13:22.

Yehova ankakonda kwambiri Davide moti ananena kuti iye anali “munthu wapamtima pake.” (1 Sam. 13:13, 14) Koma kenako Davide anachita chigololo ndi mkazi wa Uriya ndipo mkaziyu anatenga pakati. Izi zinachitika mwamuna wake ali kunkhondo. Mwamunayo atabwera, Davide anamuuza kuti apite kwawo n’cholinga choti akagone ndi mkazi wakeyo. Anachita izi kuti tchimo lakelo lisaonekere. Koma Uriya anakana ndipo Davide anakonza zoti iye aphedwe kunkhondo. Izi zinabweretsa mavuto aakulu m’banja la Davide. (2 Sam. 12:9-12) Koma Mulungu anamuchitira chifundo n’kumukhululukira chifukwa choti ankayesetsa kumutumikira ndi “mtima wosagawanika.” (1 Maf. 9:4) Kodi inuyo mukanakhala ku Isiraeli pa nthawiyo mukanatani? Kodi mukanasiya kutumikira Mulungu chifukwa cha zimene Davide anachitazi? w16.06 4:7

Loweruka, June 9

Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.—Maliko 13:33.

A Mboni za Yehovafe timaona kuti malangizo a Yesuwa ndi ofunika kwambiri. Tikudziwa kuti tili “nthawi yamapeto” yeniyeni ndipo “chisautso chachikulu” chikhoza kuyamba nthawi iliyonse. (Dan. 12:4; Mat. 24:21) Panopa uthenga wa Ufumu ukulalikidwa padziko lonse. Komanso zinthu monga nkhondo, makhalidwe oipa, njala, miliri ndi zivomerezi zili ponseponse. Nazonso zipembedzo zikusokoneza kwambiri anthu. (Mat. 24:7, 11, 12, 14; Luka 21:11) Tikuyembekezera nthawi imene Yesu adzabwere kudzatipulumutsa komanso kudzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu. (Maliko 13:26, 27) Koma ngakhale titayesetsa bwanji sitingadziwe chaka, tsiku kapena ola limene chisautso chachikulu chidzayambe. w16.07 2:2-4

Lamlungu, June 10

Tiyandikire mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu ndipo tipemphere kwa Mulungu ndi ufulu wa kulankhula.​—Aheb. 4:16.

Yehova watisonyezanso kukoma mtima kwakukulu potilola kuti tizipemphera kwa iye. Kuti zimenezi zitheke, Yehova watipatsa Mwana wake ndipo “kudzera mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula ndiponso njira yofikira Mulungu popanda kukayikira pokhala ndi chikhulupiriro mwa Yesuyo.” (Aef. 3:12) Apa tinganenedi kuti Yehova watisonyeza kukoma mtima kwakukulu. Paulo ananena kuti tiyenera kupemphera momasuka kwa Yehova kuti “atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:16b) Pa nthawi iliyonse imene tapanikizika ndi mavuto tingathe kupemphera kwa Yehova kuti atichitire chifundo n’kutithandiza. Mwa chisomo chake amatiyankha ndipo nthawi zambiri amagwiritsira ntchito Akhristu anzathu. Izi zimatithandiza kuti “tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”​—Aheb. 13:6. w16.07 3:12, 13

Lolemba, June 11

Sara anali womvera kwa Abulahamu, ndipo anali kumutcha kuti “mbuyanga.” Tsopano inuyo mwakhala ana ake.​—1 Pet. 3:6.

Nowa anali ndi mkazi mmodzi. N’chimodzimodzinso ana ake atatu aja. Koma anthu ena pa nthawiyo ankakwatira mitala. M’zikhalidwe zambiri kuchita chiwerewere sinali nkhani ndipo ena ankaona kuti ndi mbali ya chipembedzo chawo. Pa nthawi imene Abulahamu ndi Sara ankafika ku Kanani, anthu ambiri m’dzikolo anali ndi makhalidwe oipa osalemekeza ukwati. Choncho Yehova analamula kuti mizinda ya Sodomu ndi Gomora iwonongedwe chifukwa anthu a m’mizindayi ankachita komanso kulekerera zinthu zachiwerewere zoipa kwambiri. Koma Abulahamu ankatsogolera bwino banja lake ndipo Sara ankapereka chitsanzo chabwino pogonjera mwamuna wakeyo. (1 Pet. 3:3-5) Abulahamu anaonetsetsanso kuti mwana wake Isaki akwatire mkazi wolambira Yehova. Nayenso Yakobo ankachita zinthu zogwirizana ndi kulambira koona. Yakobo ndi amene anadzakhala kholo la mafuko 12 a Isiraeli. w16.08 1:10

Lachiwiri, June 12

Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.​—Yes. 60:22.

Mawu amenewa akukwaniritsidwa masiku otsiriza ano. Tikutero chifukwa chakuti m’chaka chautumiki cha 2015, padziko lonse panali ofalitsa okwana 8,220,105. Koma munthu aliyense ayenera kuganizira mawu omaliza a m’vesili. Paja Atate wathu wakumwamba ananena kuti: “Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” Panopa zili ngati tili m’galimoto yomwe yayamba kuthamanga kwambiri chifukwa ntchito yolalikira ikuchitika mwamsanga kwabasi. Kodi inuyo panokha mukuchita zonse zimene mungathe pa ntchito yolalikira? Abale ndi alongo ambiri akuyamba upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Komanso ambiri akusamukira m’madera amene kukufunika ofalitsa ambiri. Kaya ndinu m’bale kapena mlongo, pali zinthu zambiri zimene mungachite “mu ntchito ya Ambuye.”​—1 Akor. 15:58. w16.08 3:1, 2

Lachitatu, June 13

Dzanja la Yehova silinafupike moti n’kulephera kupulumutsa.—Yes. 59:1.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, Aamaleki anabwera kudzamenyana nawo. Yoswa anatsatira malangizo a Mose ndipo anatsogolera asilikali achiisiraeli ku nkhondo. Koma Mose anatenga Aroni ndi Hura n’kupita paphiri ndipo ankatha kuona malo amene nkhondoyo inkachitikira. Mose anachita zinthu zimene zinathandiza Aisiraeli kuti apambane. Iye ananyamula ndodo ya Mulungu woona. Mose akakweza m’mwamba ndodoyo, Yehova ankathandiza Aisiraeli kuti azigonjetsa Aamaleki. Koma manja ake akatopa n’kuyamba kugwa pansi, Aamaleki ankayamba kupambana. Aroni ndi Hura ataona zimenezi, nthawi yomweyo “anatenga mwala ndi kumuikira, ndipo anakhalapo.” Iwo “anachirikiza manja ake, wina mbali ina winanso mbali ina, moti manja ake anakhalabe choncho mpaka dzuwa kulowa.” Choncho Aisiraeli anapambana nkhondoyo chifukwa Mulungu anawathandiza ndi dzanja lake lamphamvu.​—Eks. 17:8-13. w16.09 1:5-7

Lachinayi, June 14

Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.​—Aroma 7:21.

Paulo ankadziwa bwino kuti kulimbana ndi zimene timalakwitsa si nkhani yamasewera chifukwa nayenso ankavutika. Koma iye ankakhulupirira kuti akhoza kupambana pa nkhondoyo ngati angadalire Yehova komanso kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. Ifenso tikhoza kupambana pa nkhondo imeneyi. Chofunika ndi kutsanzira Paulo basi. Tizidaliranso kwambiri Yehova osati mphamvu zathu ndipo tizikhulupirira kwambiri dipo. Koma nthawi zina Yehova amafuna kuti tisonyeze kuti timamudaliradi. Tiyerekeze kuti inuyo kapena munthu wina wa m’banja lanu akudwala kapenanso wachitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Kodi mungatani? Kodi mudzasonyeza kuti mumadalira Yehova popemphera mochonderera kuti akupatseni mphamvu n’cholinga choti mukhalebe okhulupirika, osangalala komanso olimba mwauzimu? (Afil. 4:13) Zitsanzo zakale komanso za masiku ano zikusonyeza kuti pemphero lingatithandize kupezanso mphamvu n’kumapirirabe mavuto athu. w16.09 2:14, 15

Lachisanu, June 15

Ayuda olankhula Chigiriki anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chiheberi.​—Mac. 6:1.

Mpingo wachikhristu utayamba kukula, panabuka nkhani ina yokhudza tsankho. Ayuda olankhula Chigiriki ankadandaula kuti akazi amasiye achigiriki akunyalanyazidwa pogawa chakudya. Pofuna kuthetsa nkhaniyi, atumwi anasankha amuna 7 kuti athandize pogawa chakudyacho mosakondera. Amuna 7 onsewo anali ndi mayina achigiriki ndipo izi zikusonyeza kuti atumwiwo ankafuna kuthetseratu nkhani yoti Akhristu a mtundu wina akusalidwa. (Mac. 6:2-6) Anthufe nthawi zonse timatengera chikhalidwe cha kumene takulira. (Aroma 12:2) Ndipo timamva anzathu kunyumba, kuntchito kapena kusukulu akunyoza anthu a mtundu wina. Kodi inuyo mumamva bwanji anthu akamanena zimenezi? Nanga mumamva bwanji munthu wina akamanyoza mtundu wanu kapena chikhalidwe chanu? w16.10 1:7, 8

Loweruka, June 16

Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.​—Aroma 1:20.

“Kuzindikira” kumatanthauza kudziwa zinthu zimene si zoonekeratu. (Aheb. 11:3) Choncho anthu ozindikira akaona kapena kumva zinthu amaziganizira kwambiri. Mwachitsanzo, tingathe kuona Mlengi wathu ndi maso achikhulupiriro tikaona zimene asayansi atulukira masiku ano. (Aheb. 11:27) Gulu la Yehova limatipatsa zinthu zambiri zotithandiza pa nkhani imeneyi. Zinthu zake ndi monga mavidiyo, mabuku komanso timabuku. (Mwachitsanzo pali vidiyo yakuti, The Wonders of Creation Reveal God’s Glory, buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You? komanso timabuku takuti, Was Life Created? ndi The Origin of Life​—Five Questions Worth Asking) Komanso mu Galamukani! nthawi zambiri mumakhala nkhani zofunsa asayansi komanso anthu ena omwe amafotokoza zimene zinawathandiza kuti ayambe kukhulupirira zoti kuli Mulungu. Mumakhalanso nkhani zakuti, “Kodi Zinangochitika Zokha?” ndipo zimafotokoza zinthu zachilengedwe zochititsa chidwi kwambiri. Masiku ano asayansi akamapanga zinthu zawo amayesetsa kutengera zam’chilengedwezi. w16.09 4:4, 5

Lamlungu, June 17

Anachitiridwa umboni chifukwa cha chikhulupiriro chawo.​—Aheb. 11:39.

Anthu okhulupirika amene anatchulidwa mu Aheberi chaputala 11 anamwalira Yesu Khristu yemwe ndi “mbewu,” asanatsegule njira yoti anthu ena adzapite kumwamba. (Agal. 3:16) Komabe adzaukitsidwa ndipo adzakhala m’Paradaiso. (Sal. 37:11; Yes. 26:19; Hos. 13:14) Ponena za anthu ena amene anakhalako Chikhristu chisanayambe, lemba la Aheberi 11:13 limati: “Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro, ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali ndi kuwalandira.” Anthuwa ankayembekezera dziko latsopano ndipo ankaganizira mmene angasangalalire atakhala m’dzikolo. Mmodzi mwa anthu amenewa anali Abulahamu. Yesu ananena kuti Abulahamu ‘ankasangalala’ akaganizira mmene zinthu zidzakhalire pa nthawi imeneyo. (Yoh. 8:56) N’chimodzimodzinso ndi Sara, Isaki, Yakobo ndi ena ambiri amene ankaganizira kwambiri za madalitso amene adzapeze mu Ufumu. Ufumuwu uli ngati “mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.”​—Aheb. 11:8-11. w16.10 3:4, 5

Lolemba, June 18

Muzipemphera pa chochitika chilichonse.​—Aef. 6:18.

Yehova amatipatsa mzimu woyera ndipo umatithandiza kuti tizimvetsa choonadi komanso tizisonyeza kuti timakhulupirira uthenga wabwino. (Luka 10:21) Tiyenera kumamuthokoza kwambiri chifukwa chotikokera kwa iye pogwiritsa ntchito Mwana wake yemwe ndi “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu.” (Aheb. 12:2) Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira? Tiyenera kupitirizabe kulimbitsa chikhulupiriro chathu popemphera komanso kuphunzira Mawu ake. (1 Pet. 2:2) Tiyeni tipitirizebe kusonyeza kuti timakhulupirira malonjezo a Yehova. Tizichita zinthu zimene zingathandize aliyense kuona kuti tili ndi chikhulupiriro. Mwachitsanzo, tizilalikira za Ufumu komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Tipitirizenso kuchitira “onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” (Agal. 6:10) Komanso tiziyesetsa ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.’​—Akol. 3:5, 8-10. w16.10 4:11, 12

Lachiwiri, June 19

[Yehova] anapanga kumwamba mwanzeru.​—Sal. 136:5.

Yehova analenga zinthu mwadongosolo. Izi zikusonyeza kuti iye amafunanso kuti anthu ake azichita zinthu mwadongosolo. Choncho anatipatsa Baibulo kuti lizititsogolera. Munthu amene satsatira mfundo za Mulungu komanso malangizo a gulu lake amakumana ndi mavuto ambiri ndipo sasangalala. Aisiraeli ankatsatira Chilamulo cha Mulungu ndipo ankachita zinthu mwadongosolo. Mwachitsanzo, panali akazi “amene anali kutumikira mwadongosolo pachipata cha chihema chokumanako.” (Eks. 38:8) Komanso pamene Aisiraeli ankachoka ku Iguputo ankachita zinthu mwadongosolo pochoka pamalo komanso ponyamula chihema. Kenako Mfumu Davide inakonza zoti Alevi ndi ansembe azigwira ntchito zosiyanasiyana pakachisi. (1 Mbiri 23:1-6; 24:1-3) M’nthawi ya atumwi, Yehova anathandizanso kuti mipingo izichita zinthu mwadongosolo. Panali bungwe lolamulira limene linkapereka malangizo oti mipingoyo izitsatira ndipo poyamba atumwi ndi amene anali m’bungweli. (Mac. 6:1-6) Mipingo inkalandiranso malangizo kudzera m’makalata ouziridwa.​—1 Tim. 3:1-13; Tito 1:5-9. w16.11 2:3, 6, 8, 9

Lachitatu, June 20

Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo atengedwe kupita ku ukapolo!​—Yer. 15:2.

M’chaka cha 607 B.C.E., asilikali a Babulo motsogoleredwa ndi Mfumu Nebukadinezara Yachiwiri anapita kukawononga mzinda wa Yerusalemu. Pofotokoza zimene zinachitika, Baibulo limati: “[Mfumu Nebukadinezara] inapha anyamata awo ndi lupanga m’nyumba yopatulika. Sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu. . . . Inatentha nyumba ya Mulungu woona ndi kugwetsa mpanda wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino, mpaka zonse zinawonongedwa.”(2 Mbiri 36:17, 19) Anthu okhala mu Yerusalemu sankayenera kudabwa pamene mzindawo unawonongedwa. Kwa zaka zambiri, aneneri a Mulungu anali atachenjeza Ayuda kuti akapanda kumvera Yehova, Ababulo adzawatenga n’kupita nawo ku ukapolo. Aneneriwo anafotokoza kuti Ayuda ambiri adzaphedwa ndi lupanga ndipo amene adzapulumuke adzakhala ku ukapolo kwa moyo wonse. w16.11 4:1, 2

Lachinayi, June 21

Uchimo [unalowa] m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi.​—Aroma 5:12.

“Munthu mmodzi” wotchulidwa pa Aroma 5:12 ndi Adamu ndipo kudzera mwa iye uchimo ndi imfa ‘zinalowa m’dziko.’ Choncho “chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo imfa inalamulira monga mfumu.” Koma Paulo ananenanso kuti “kukoma mtima kwakukulu kochuluka [kwa Mulungu]” kunaoneka “kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.” (Aroma 5:12, 15, 17) Ndipo kukoma mtima kwakukulu kumeneku kwathandiza kwambiri anthu onse. Tikutero chifukwa “kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu [Yesu], ambiri adzakhala olungama.” Izi zikusonyeza kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kudzachititsa kuti “moyo wosatha ubwere kudzera mwa Yesu Khristu.” (Aroma 5:19, 21) Yehova sankafunikira kutumiza Mwana wake kudzapereka dipo. Koma anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu pokonza njira yotipulumutsira ku uchimo ndi imfa. Anthu ochimwafe tinali osayenera kupatsidwa dipo ndi Mulungu komanso Yesu. Choncho timayamikira kwambiri zimene anachitazi chifukwa zimathandiza kuti machimo athu azikhululukidwa komanso kuti tidzakhale ndi moyo wosatha. Koma kodi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti timayamikiradi zomwe Mulungu anachitazi? w16.12 1:1, 6, 7

Lachisanu, June 22

Kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani ndi Mulungu, popeza thupi siligonjera chilamulo cha Mulungu.​—Aroma 8:7.

N’chifukwa chiyani tiyenera kudzifufuza pa nkhaniyi? Paulo analemba kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa.” (Aroma 8:6) Izitu n’zoopsa chifukwa munthu angafe pawiri. Panopa angafe mwauzimu ndipo m’tsogolomu sadzapeza moyo wosatha. Koma mawu a Paulowa sakutanthauza kuti munthu akangoyamba “kuika maganizo pa zinthu za thupi” ndiye kuti afa basi. N’zotheka kusintha. Chitsanzo ndi munthu wa ku Korinto amene ankatsatira zofuna za thupi mpaka kufika pochotsedwa mumpingo. Mwayi wosintha unalipo ndipo anasinthadi. Iye anasiya kutsatira zofuna za thupi ndipo anayamba kuchita zabwino. (2 Akor. 2:6-8) Ngati munthu wa ku Korintoyu anali ndi mwayi wosintha, ndiye kuti masiku ano mwayiwu uliponso. N’zotheka ndithu kuti Mkhristu amene wayamba kutsatira zofuna za thupi asinthe. Choncho mfundo yoti “kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa” iyenera kulimbikitsa Mkhristu aliyense kusintha moyo wake. w16.12 2:5, 12, 13

Loweruka, June 23

Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.​—Sal. 55:22.

Kunena zoona timalimbikitsidwa ‘tikatulira Yehova nkhawa zathu’ chifukwa timadziwa kuti atithandiza. Tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Taganizirani mfundo imeneyi. Mulungu angathe kuchita, osati chabe zazikulu, koma “zazikulu kwambiri.” Kuti tidzalandire mphoto, tiyenera kukhulupirira Yehova komanso kumvera malangizo ake. Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova adzakudalitsa ndithu m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako. Adzakudalitsa ngati udzamveradi mawu a Yehova Mulungu wako ndi kutsatiradi malamulo onsewa amene ndikukupatsa lero. Yehova Mulungu wako adzakudalitsa ndithu monga mmene anakulonjezera.” (Deut. 15:4-6) Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yehova angakudalitseni mukamamutumikira ndi mtima wonse? Pali zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira zimenezi. w16.12 4:8, 9

Lamlungu, June 24

Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera.​—Deut. 7:6.

Sikuti Yehova anangosankha mtundu wa Aisiraeli popanda chifukwa. Anachita zimenezi pofuna kukwaniritsa lonjezo limene anapangana ndi bwenzi lake Abulahamu. (Gen. 22:15-18) Nthawi zonse Yehova amagwiritsa ntchito ufulu wake wosankha zochita mogwirizana ndi chikondi komanso chilungamo. Umboni wa izi ndi zimene ankachita ndi Aisiraeli. Iwo mobwerezabwereza ankasiya kulambira koona. Koma akalapa, Yehova ankawasonyeza chifundo. Iye anati: “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga.” (Hos. 14:4) Apatu Yehova ankagwiritsa ntchito ufulu wake wosankha kuti athandize ena. Yehova atayamba ntchito yolenga, anasankha kuti apatse angelo ufulu wosankha zochita. Mngelo woyamba kulandira ufuluwu anali Mwana wake amenenso ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (Akol. 1:15) Kodi Yesu amagwiritsa ntchito bwanji ufuluwu? Asanabwere padzikoli anasankha kukhalabe wokhulupirika kwa Atate wake ndipo sanakhale kumbali ya Satana. w17.01 2:3, 4

Lolemba, June 25

Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.​—Aheb. 6:10.

Utumiki wathu ukhoza kusintha mwina chifukwa cha zinthu zina zimene zachitika pa moyo wathu. Tikhoza kupezeka kuti tayamba kuchita zambiri kapena zochepa. Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, timadwaladwala kapena ayi, Yehova amatiganizira ndipo amadziwa zimene aliyense angachite pomutumikira. Iye sayembekezera zimene sitingakwanitse ndipo amayamikira zimene timayesetsa kumuchitira. Yesu ankasangalala ndi utumiki uliwonse umene anapatsidwa ndipo ifenso tikhoza kumasangalala ndi utumiki wathu. (Miy. 8:30, 31) Munthu wodzichepetsa amakhutira ndi utumiki kapena udindo umene ali nawo. Iye sadandaula kuti sanapatsidwe utumiki winawake kapena kuti anzake apatsidwa udindo wina. M’malomwake amasangalala ndi utumiki wake n’kumauchita mwakhama podziwa kuti wachokera kwa Yehova. Komanso amalemekeza anthu amene apatsidwa udindo ndipo amawathandiza podziwa kuti udindo wawowo wachokeranso kwa Yehova.​—Aroma 12:10. w17.01 3:13, 14

Lachiwiri, June 26

Monga mwana ndi bambo ake, watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.​—Afil. 2:22.

Masiku ano, abale ena achinyamata akuyang’anira ntchito zimene zikugwiridwa ndi achikulire. Zikatere, achinyamatawo ayenera kufunsira nzeru kwa achikulirewo asanasankhe zochita. Timoteyo ali wachinyamata anatumikira ndi mtumwi Paulo kwa zaka zambiri. Paulo analembera Akorinto kuti: “Ndikukutumizirani Timoteyo, popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu, monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse.” (1 Akor. 4:17) Mawuwa akusonyeza kuti Paulo ndi Timoteyo ankagwira ntchito limodzi mogwirizana. Paulo anayesetsa kupeza nthawi yophunzitsa Timoteyo ‘mmene ankachitira zinthu potumikira Khristu.’ Timoteyo anaphunzira zambiri ndipo Paulo ankamukonda. Ndipotu Paulo ankakhulupirira kuti Timoteyo angathe kuthandiza Akorinto. Zimenezi ndi chitsanzo chabwino kwa akulu akamaphunzitsa ena kuti akhale oyang’anira. w17.01 5:13, 14

Lachitatu, June 27

Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.​—Mac. 24:15.

Yehova amafuna kuti anthu azikhala ndi moyo osati azifa. Popeza iye ndi kasupe wa moyo, adzakhala Atate wa onse amene adzaukitsidwe. (Sal. 36:9) M’pake kuti Yesu anati tizipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba.” (Mat. 6:9) Yehova wapatsa Yesu ntchito yofunika kwambiri youkitsa akufa. (Yoh. 6:40, 44) M’Paradaiso, Yesu adzakwaniritsa udindo wake wokhala “kuuka ndi moyo.” (Yoh. 11:25) Yehova amasonyeza kukoma mtima kwake mopanda tsankho. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.” (Maliko 3:35) Cholinga cha Mulungu n’choti “khamu lalikulu” kapena kuti anthu osawerengeka ochokera mu fuko lililonse, mtundu uliwonse komanso chinenero chilichonse azimulambira. Anthu onse amene amakhulupirira dipo la Khristu komanso amene amachita zimene Mulungu amafuna angadzakhale m’gulu lomwe lidzafuule kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”​—Chiv. 7:9, 10. w17.02 2:10, 11

Lachinayi, June 28

Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu.​—Aheb. 13:7.

Pofuna kuti uthenga wa m’Baibulo uzilalikidwa m’zilankhulo zosiyanasiyana, mu 1884 panakhazikitsidwa bungwe la Zion’s Watch Tower Tract Society ndipo Charles Taze Russell ndi amene anali pulezidenti wake. Iye ankaphunzira Baibulo mwakhama ndipo sankaopa kutsutsa mabodza monga oti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi komanso zoti munthu akafa chinachake chimakhalabe moyo. Iye anazindikiranso kuti kubwera kwa Yesu kudzakhala kosaoneka ndiponso kuti “nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu” zidzatha mu 1914. (Luka 21:24) M’bale Russell ankagwiritsa ntchito nthawi yake, mphamvu zake komanso ndalama zake mosaumira pothandiza anthu kudziwa mfundo zimenezi. N’zodziwikiratu kuti pa nthawiyo, Yehova ndi Yesu ankagwiritsa ntchito M’bale Russell potsogolera mpingo. M’bale Russell sankafuna kuti anthu azimutamanda. Mu 1896, iye analemba kuti: “Sitikufuna kuti anthu azititamanda kapena azitamanda mabuku athu. Sitikufunanso kuti anthu azititchula kuti Abusa kapena Arabi kapena kuti anthu azidziwika ndi mayina athu.” Kenako ananena kuti: “Ntchitoyi si ya munthu.” w17.02 4:8, 9

Lachisanu, June 29

Nzeru za munthu wochenjera ndizo kuzindikira njira imene akuyendamo.​—Miy. 14:8.

Tonsefe timafunika kusankha zochita. N’zoona kuti zosankha zina sizikhala zazikulu. Koma zosankha zambiri zimakhudza kwambiri moyo wathu. Tikasankha zochita mwanzeru zinthu zimatiyendera bwino. Koma tikapanda kusankha bwino timakumana ndi mavuto. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru? Tiyenera kukhulupirira Mulungu ndipo tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti angatithandize kuti tisankhe zoyenera. Tizikhulupiriranso Mawu ake komanso tizidziwa kuti malangizo ake ndi odalirika. (Yak. 1:5-8) Ubwenzi wathu ndi Yehova ukamalimba komanso tikamakonda kwambiri Mawu ake timayamba kumudalira kwambiri podziwa kuti amatifunira zabwino. Zikatere, nthawi zonse timafufuza kaye m’Mawu ake tisanasankhe zochita. w17.03 2:2, 3

Loweruka, June 30

Maso athu ali pa inu.​—2 Mbiri 20:12.

Mofanana ndi bambo ake, Yehosafati anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu pa nthawi imene adani oopsa anabwera. (2 Mbiri 20:2-4) N’zoona kuti Yehosafati anachita mantha. Koma “anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.” Iye anapemphera modzichepetsa n’kunena kuti anthu ake alibe “mphamvu zotha kulimbana ndi khamu lalikulu.” Ananenanso kuti iye ndi anthu akewo sankadziwa zochita. Posonyeza kuti ankadalira Yehova, Yehosafati ananena mawu amulemba la lero. Nthawi zina ifenso tikhoza kuchita mantha mpaka kufika posowa zochita. (2 Akor. 4:8, 9) Koma mfundo yoyenera kuikumbukira ndi yoti Yehosafati anapemphera pagulu n’kufotokoza mmene zinthu zinalili. (2 Mbiri 20:5) Amunanso ayenera kutsanzira Yehosafati n’kumapempha Yehova kuti awapatse nzeru komanso mphamvu zowathandiza pa vuto limene akumana nalo. Mukamapemphera ndi banja lanu musamachite manyazi kutchula mavuto amene akukudetsani nkhawa. Mukamatero iwo amadziwa kuti mumadalira Yehova. Kumbukirani kuti Yehova anathandiza Yehosafati choncho akhoza kukuthandizaninso inuyo. w17.03 3:12, 13

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena