July
Lamlungu, July 1
Ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.—Ower. 11:36.
Mwana wa Yefita analolera kuti asakwatiwe ndiponso kuti asakhale ndi ana n’cholinga choti azitumikira Yehova. Kodi ifeyo tingamutsanzire bwanji? Masiku anonso, abale ndi alongo achinyamata amalolera kuti asalowe m’banja kapena asakhale ndi ana kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Palinso achikulire ena amene amadzipereka kwambiri. Amalolera kusiya ana ndi zidzukulu kuti agwire ntchito zomangamanga, alowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu kapena akalalikire kudera lina. Pa nthawi yoitanira anthu ku Chikumbutso abale ndi alongo enanso amayesetsa kuti akhale ndi nthawi yambiri yogawira nawo timapepala. Yehova amasangalala akamaona zonsezi ndipo sadzaiwala ntchito yawo komanso chikondi chimene amachisonyeza. (Aheb. 6:10-12) Kodi nanunso mukhoza kuwonjezera zimene mumachita potumikira Yehova? w16.04 1:16, 17
Lolemba, July 2
Zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.—Yoh. 10:16.
Yesu anati iyeyo ndi m’busa ndipo otsatira ake ndi gulu la nkhosa. Ndiye taganizirani izi, tiyerekeze kuti nkhosa ziwiri zili paphiri, ziwiri zili m’chigwa ndipo imodzi ikudya kudambo. Kodi tinganene kuti limeneli ndi gulu la nkhosa? Ayi. Nkhosa zimapanga gulu zikakhala pamodzi ndipo m’busa akhoza kuzitsogolera bwino. Mofanana ndi zimenezi, sitingatsatire m’busa wathu ngati tili ndi chizolowezi chosafika pamisonkhano. Tiyenera kusonkhana ndi Akhristu anzathu kuti tikhale nawo m’gulu lotsogoleredwa ndi “m’busa mmodzi.” Komanso tikamasonkhana timakhala ngati banja limodzi logwirizana. (Sal. 133:1) Abale ndi alongo athu ena anakanidwa ndi makolo ndiponso achibale awo. Koma Yesu analonjeza anthu oterewa kuti adzawapatsa anthu oti aziwakonda komanso kuwasamalira. (Maliko 10:29, 30) Ndiyeno, tikamafika pamisonkhano timakhala bambo, mayi, mchimwene ndiponso mchemwali wa abale ndi alongowa. Kuganizira kwambiri mfundoyi kungatithandize kuti tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano nthawi zonse. w16.04 3:9, 10
Lachiwiri, July 3
Ndipo mukaimirira n’kumapemphera, khululukani chilichonse chimene wina anakulakwirani kuti Atate wanu wakumwamba akukhululukireni machimo anunso.—Maliko 11:25.
Ngati sitingakhale mwamtendere ndi anthu ena, zinthu zimene timachita potumikira Yehova monga kupemphera, kusonkhana ndi kulalikira zimakhala zopanda phindu. Sitingathe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngati sitikhululukira anzathu. (Luka 11:4; Aef. 4:32) Mkhristu aliyense ayenera kudzifufuza kuti aone ngati amakhululukadi komanso kukhala mwamtendere ndi ena. Kodi ena akakulakwirani mumawakhululukira ndi mtima wonse? Nanga mumayambanso kucheza nawo ngati kale? Yehova amafuna kuti atumiki ake azikhululukira ena. Ngati mukuona kuti pali zimene muyenera kusintha, pemphani Yehova kuti akuthandizeni ndipo iye adzayankha pemphero lanulo.—1 Yoh. 5:14, 15. w16.05 1:6, 7
Lachitatu, July 4
Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa.—Mat. 24:14.
Kodi ntchitoyi tiigwira mpaka liti? Yesu ananena kuti idzagwiridwa mpaka m’masiku otsiriza “kenako mapeto adzafika.” Kodi pali chipembedzo chinanso chimene chikugwirabe ntchito yolalikira uthenga wabwino m’masiku otsiriza ano? Anthu ena amanena kuti, “Inu mumagwira ntchito yolalikira koma ife tili ndi mzimu woyera.” Koma kodi kugwirabe ntchito yolalikira si umboni wakuti tili ndi mzimu wa Mulungu? (Mac. 1:8; 1 Pet. 4:14) Anthu a zipembedzo zina ayesapo kuchita zimene a Mboni za Yehova amachita koma alephera. Ena amachita umishonale kwakanthawi, kenako n’kusiya. Ndipo ena amalalikira kunyumba ndi nyumba koma uthenga umene amalalikira umakhala wosiyana ndi umene Yesu ankalalikira. w16.05 2:13, 16
Lachinayi, July 5
Abale, ndikuti pitirizani kukondwera, kusintha maganizo anu, kulimbikitsidwa, kukhala ndi maganizo ogwirizana, ndiponso kukhala mwamtendere.—2 Akor. 13:11.
Pamafunika khama kuti munthu ‘asinthe maganizo’ ndi “kuvala umunthu watsopano.” Paulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale, umenenso ukuipitsidwa malinga ndi zilakolako zonyenga za umunthuwo. Ndipo munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aef. 4:22-24) Mawu akuti “mukhale atsopano,” akusonyeza kuti kuvala umunthuwu kuyenera kuchitika mopitirizabe. Zimenezi n’zolimbikitsa chifukwa zikusonyeza kuti kaya tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tingathe kumasinthabe. Baibulo lingatithandize kuti tipitirize kusintha. w16.05 4:8, 9
Lachisanu, July 6
Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda.—Miy. 3:12.
Yehova akutiumbira mu paradaiso wauzimu ndipo timaona kuti ndife otetezeka kudziko loipali. (Yes. 64:8) Tonsefe tadziwa Mulungu ndipo timaona kuti amatikonda monga Atate athu. (Yak. 4:8) M’dziko latsopano tidzasangalala kwambiri chifukwa tidzakhala m’paradaiso weniweni ndipo Ufumu wa Mulungu ndi umene uzidzatilamulira. Pa nthawiyo Yehova adzapitiriza kutiumba ndiponso kutiphunzitsa zinthu zambiri. (Yes. 11:9) Adzatithandizanso kukhala ndi maganizo ndiponso matupi angwiro kuti tizidzatha kumvetsa bwino zimene azidzatiphunzitsa komanso tizidzamutumikira osalakwitsa chilichonse. Choncho tiyeni tipitirize kumvera Yehova ndipo tizidziwa kuti amatiumba chifukwa choti amatikonda kwambiri. w16.06 1:8, 9
Loweruka, July 7
Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.—Deut. 6:4.
Mawu amenewa ananena ndi Mose m’chaka cha 1473 B.C.E. potsanzikana ndi Aisiraeli m’chigwa cha Mowabu. Aisiraeli anali atatsala pang’ono kuwoloka mtsinje wa Yorodano kuti akalandire Dziko Lolonjezedwa. (Deut. 6:1) Mose anali atawatsogolera kwa zaka 40, ndipo ankafuna kuti iwo akhale olimba mtima. Aisiraeli ankafunika kukhulupirira Yehova Mulungu wawo ndiponso kumumvera. Mawu a Mosewa ayenera kuti anawalimbikitsa kwambiri. Mose atatchula Malamulo Khumi komanso malamulo ena, ananena mawu a pa Deuteronomo 6:4, 5. Pa nthawiyo Aisiraeli anali atadziwa kale kuti Mulungu amene amamulambira ndi “Yehova mmodzi” ndipo ndi Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. w16.06 3:2, 3
Lamlungu, July 8
Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.—Mat. 24:36.
Yesu ananena mawu amenewa pamene anali pazikoli. Koma panopa iye wapatsidwa mphamvu kuti awononge dziko la Satanali. (Chiv. 19:11-16) Choncho tikhoza kunena kuti akudziwa nthawi imene Aramagedo idzayambe. Koma ifeyo sitikudziwa nthawi yake. Ndiyetu m’pake kuti tiyenera kukhala maso mpaka pamene chisautso chidzayambe. Yehova akudziwa nthawi yeniyeni pamene chisautso chidzayambe. Nthawiyo ikuyandikirayandikirabe ndipo Baibulo limanena kuti ‘siidzachedwa.’ (Hab. 2:1-3) Kodi tingatsimikize bwanji zimenezi? Yehova amakwaniritsa chilichonse chimene walonjeza pa nthawi yake yeniyeni. Nafenso tisamakayikire zoti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzatipulumutsa pa chisautso chachikulu. Koma kuti tidzapulumuke tiyenera kupitirizabe kukhala maso. w16.07 2:4-6
Lolemba, July 9
Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, koma ine ndekha sindidzatero.—Maliko 14:29.
Petulo ananena kuti ngakhale atumwi enawo atamusiya Yesu, iye sadzamusiya. (Maliko 14:27-31, 50) Koma pamene Yesu ankagwidwa, atumwi onse, ndi Petulo yemwe, anamuthawa. Komanso iye anakana katatu zoti amadziwa Yesu. (Maliko 14:53, 54, 66-72) Komabe Petulo analapa machimo akewa ndipo Yehova anapitiriza kumugwiritsa ntchito. Inuyo mukanakhala mmodzi wa ophunzira pa nthawiyo, kodi mukanatani? Kodi mukanasiya kutumikira Mulungu chifukwa cha zimene Petulo anachitazi? Kodi panopa mumazindikira kuti Yehova ndi wachifundo ndipo angapereke mpata kwa munthu woti alape? Nanga mumakhulupirira kuti iye amakonza zinthu pa nthawi yake komanso moyenera? Nthawi zinanso munthu amene wachita tchimo angasonyeze kuti sakuzindikira kulakwa kwake ndipo sangalape. Zikatere, kodi mungakhale ndi chikhulupiriro choti Yehova adzaweruza munthuyo pa nthawi yake mwinanso kuchititsa kuti achotsedwe? w16.06 4:8, 9
Lachiwiri, July 10
Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, . . . alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani.—2 Ates. 2:16, 17.
Yehova amatilimbikitsanso tikakhala ndi nkhawa. (Sal. 51:17) M’kalata imene Paulo analembera Atesalonika amene ankazunzidwa, ananena mawu amulemba la leroli.Timayamikira kwambiri kuti Yehova ndi wokoma mtima ndipo amatilimbikitsa mwachikondi. Anthu ochimwafe tinalibe chiyembekezo chilichonse. (Sal. 49:7, 8) Koma Yehova watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri. Paja Yesu analonjeza otsatira ake kuti: “Chifuniro cha Atate wanga ndi chakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupirira mwa iye akhale nawo moyo wosatha.” (Yoh. 6:40) Kunena zoona, chiyembekezochi ndi mphatso yamtengo wapatali imene timaipeza chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Paulo ankadziwa bwino mfundoyi ndipo anati: “Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweretsa chipulumutso kwa anthu, kaya akhale a mtundu wotani.”—Tito 2:11. w16.07 3:14, 15
Lachitatu, July 11
Musachitire zachinyengo akazi anu amene munawakwatira muli anyamata.—Mal. 2:15.
Mpingo wachikhristu sulekerera munthu aliyense wochita chinyengo m’banja. Koma tiyerekeze kuti Mkhristu wina wapabanja wayamba chibwenzi ndi mwamuna kapena mkazi wa munthu wina. Kenako akuthetsa banja lake n’kukwatirana ndi chibwenzicho. N’zoona kuti zoterezi sizichitikachitika pakati pa Akhristu. Koma ngati Mkhristu wotereyu atapanda kulapa, angachotsedwe mumpingo n’cholinga choti mpingowo ukhalebe woyera. (1 Akor. 5:11-13) Kuti abwezeretsedwe, ayenera kuonetsa ‘zipatso zosonyeza kuti walapa.’ (Luka 3:8; 2 Akor. 2:5-10) N’zoona kuti palibe lamulo loti payenera kupita nthawi yakutiyakuti kuti munthuyo abwezeretsedwe. Komabe asanabwezeretsedwe, pamafunika kuiganizira bwino nkhaniyo ndiponso zimene anachitazo. Mwina pangatenge chaka kapena kuposa, kuti munthuyo asonyeze kuti walapadi. Koma ngakhale munthu wotereyu atabwezeretsedwa, ayenera kudziwa kuti adzayankhabe mlandu “pa mpando woweruzira milandu wa Mulungu.”—Aroma 14:10-12. w16.08 1:12, 13
Lachinayi, July 12
Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino.—1 Tim. 3:1.
Mawu akuti ‘kuyesetsa’ omwe ali palembali, amatanthauza kunyanyamphira kuti ufikire chinthu chimene chili patali. Paulo anagwiritsa ntchito mawuwa pofuna kusonyeza kuti pamafunika khama kuti munthu ayenerere udindo komanso kuti azichita zambiri m’gulu la Yehova. Tiyerekeze kuti m’bale wina akuganizira zimene angachite mumpingo wawo. Iye si mtumiki wothandiza ndipo akuzindikira kuti choyamba ayenera kuyesetsa kuti akhale ndi makhalidwe achikhristu. Kenako akuyesetsa kuti akhale mtumiki wothandiza. Patapita nthawi akuyesetsanso kuti akhale mkulu. Nthawi zonse amayesetsa kukwaniritsa zofunika kuti akhale pa udindo umene akufunawo. N’chimodzimodzinso ndi abale komanso alongo amene akufuna kukhala apainiya, kukatumikira pa Beteli komanso kugwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Iwo ayenera kuyesetsa kuti akwaniritse zolinga zawozi. w16.08 3:3, 4
Lachisanu, July 13
Iwo ndi atumiki anu ndi anthu anu, amene munawawombola ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.—Neh. 1:10.
Nehemiya atapita ku Yerusalemu anapeza zinthu zitasokonekera. Chitetezo cha mzindawo sichinali bwino ndipo Ayuda ena anali atagwa ulesi. Iwo ataopsezedwa ndi anthu a mitundu ina, anasiya kugwira ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. Kodi izi zinafooketsanso Nehemiya? Ayi. Iye anachita zinthu mofanana ndi Mose, Asa komanso atumiki ena okhulupirika. (Eks. 17:8-13; 2 Mbiri 14:8-13) Izi zinatheka chifukwa chakuti iye anali ndi chizolowezi chodalira Yehova ndipo n’zimenenso anachita pa nthawiyi. Nehemiya anapemphera kwa Yehova ndipo iye anathandiza Ayuda kuthana ndi vuto limene linkaoneka ngati losatheka. Mulungu anagwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu komanso ‘dzanja lake lamphamvu’ polimbitsa manja a Ayuda amene anafooka. (Neh. 2:17-20; 6:9) Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yehova amagwiritsa ntchito ‘mphamvu zake zazikulu’ komanso ‘dzanja lake lamphamvu’ polimbikitsa atumiki ake masiku ano? w16.09 1:9
Loweruka, July 14
Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.—1 Akor. 10:31.
Mtolankhani wa nyuzipepala ina anafotokoza mmene anthu anavalira pamsonkhano wina wa atsogoleri azipembedzo. Anati: “Ambiri anavala motayirira chifukwa kunkatentha.” Koma ponena za a Mboni, iye anati: “Pamsonkhano wa Mboni za Yehova. . . . Amuna amavala majekete ndi mataye pamene akazi amavala masiketi aatali bwino . . . komanso okongola.” A Mboni za Yehova nthawi zonse amayamikiridwa kuti ‘amadzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru . . . mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera.’ (1 Tim. 2:9, 10) Palembali Paulo ankanena za akazi koma mfundo zake zikugwiranso ntchito kwa amuna. Akhristufe timaona kuti kuvala zoyenera n’kofunika chifukwa ndi zimene Yehova Mulungu amene timamulambira amafuna. (Gen. 3:21) Zimene Malemba amanena pa nkhaniyi, zimasonyeza kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azivala mosiyana ndi anthu a m’dzikoli. Choncho pa nkhani ya zovala, tiziganiziranso zimene zingasangalatse Ambuye Wamkulu Koposa. w16.09 3:1, 2
Lamlungu, July 15
Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.—2 Pet. 1:21.
Anthu ena amasankha kuti afufuze maulosi a m’Baibulo kapena umboni woti ndi lolondola pa nkhani za sayansi kapena mbiri yakale. Ulosi wina wochititsa chidwi ndi wopezeka pa Genesis 3:15. Vesili limafotokoza mwachidule nkhani yaikulu m’Baibulo. Nkhani yake ndi yokhudza ulamuliro wa Yehova komanso mmene Ufumu udzayeretsere dzina lake. Pavesi limodzi lokhali Mulungu anafotokoza mophiphiritsira mmene adzathetsere mavuto onse amene anayamba mu Edeni. Kodi mungachite zinthu ziti pophunzira vesili? Mwina mungayambe ndi kulemba mzere wosonyeza nthawi. Kenako pamzerepo mungalembe mavesi komanso zinthu zimene Mulungu ananena pang’onopang’ono zosonyeza kuti ulosiwu udzakwaniritsidwa. Mukaona kugwirizana kwa malembawo, mungayambe kukhulupirira kwambiri kuti aneneri ndiponso anthu amene analemba Baibulo ‘ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera.’ w16.09 4:8
Lolemba, July 16
Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena ndani?—1 Akor. 4:7.
Poyamba, mtumwi Petulo sankakonda anthu a mitundu ina koma kenako anasintha n’kuchotseratu maganizo amenewa mumtima mwake. (Mac. 10:28, 34, 35; Agal. 2:11-14) Ifenso tikazindikira kuti tili ndi kamtima ka tsankho kapena konyadira mtundu wathu, tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tikachotse. (1 Pet. 1:22) Kaya ndife a mtundu uti, tizikumbukira kuti tonsefe ndi ochimwa ndipo tinali osayenera kupulumuka. (Aroma 3:9, 10, 21-24) Ndiye ngati zili choncho, kodi pali chifukwa choganizira kuti timaposa anzathu? Tiyenera kukhala ndi maganizo amene mtumwi Paulo anali nawo. Paja iye anauza anzake odzozedwa kuti iwo sanalinso ‘anthu osadziwika kapena alendo m’dziko la eni, koma a m’banja la Mulungu.’ (Aef. 2:19) Tikamayesetsa kuthetsa maganizo a tsankho, tidzatha kuvala umunthu watsopano.—Akol. 3:10, 11. w16.10 1:9
Lachiwiri, July 17
Amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.—Sal. 1:2.
Yehova watipatsa Baibulo lathunthu kuti litithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kuti tizisangalala. Choncho ndi bwino kuyesetsa kuti tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3; Mac. 17:11) Mofanana ndi atumiki a Mulungu akale, tiyenera kuganizira kwambiri malonjezo a Yehova komanso kumvera malangizo ake. Yehova amagwiritsanso ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera. (Mat. 24:45) Tiyeni tizigwiritsa ntchito kwambiri zinthu zonse zimene Yehova amatipatsa. Tikatero tidzafanana ndi atumiki akale okhulupirika omwe ankayembekezera Ufumu wa Mulungu ndipo sankakayikira ngakhale pang’ono malonjezo ake. (Aheb. 11:1) Pemphero linkathandizanso atumiki a Yehova akale kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Akazindikira kuti Yehova wayankha mapemphero awo, iwo ankayamba kumukhulupirira ndi mtima wonse.—Neh. 1:4, 11; Sal. 34:4, 15, 17; Dan. 9:19-21. w16.10 3:7, 8
Lachitatu, July 18
Ngati ndili ndi chikhulupiriro chonse choti n’kusuntha nacho mapiri, koma ndilibe chikondi, sindili kanthu.—1 Akor. 13:2.
Yesu ananena kuti “lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo” ndi loti tizikonda Mulungu. (Mat. 22:35-40) Chikondi ndi chikhulupiriro ndi makhalidwe awiri ofunika kwambiri. Choncho olemba Baibulo ambiri anatchula chikhulupiriro ndi chikondi mobwerezabwereza ndipo nthawi zina ankatchula makhalidwewa pamodzi. Mwachitsanzo, Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘avale chodzitetezera pachifuwa chachikhulupiriro ndi chikondi.’ (1 Ates. 5:8) Yohane analemba kuti: “Lamulo [la Mulungu] ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro m’dzina la Mwana wake Yesu Khristu ndiponso tizikondana.” (1 Yoh. 3:23) Ngakhale kuti chikhulupiriro n’chofunika, chidzatha malonjezo a Mulungu akadzakwaniritsidwa. Koma tidzapitirizabe kukonda Mulungu ndi anzathu. N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Komabe, tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.”—1 Akor. 13:13. w16.10 4:15-17
Lachinayi, July 19
Mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro.—Mac. 16:5.
Abale amene ankatumidwa ndi bungwe lolamulira ankapereka ku mipingo “malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula.” (Mac. 16:4) Mipingo ikamatsatira malamulowo, ‘inkalimba m’chikhulupiriro ndipo chiwerengero chinkapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.’ Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Kodi abale amene ali m’Makomiti a Nthambi, Makomiti a Dziko komanso oyang’anira madera ndi akulu ayenera kuchita chiyani akalandira malangizo ochokera ku gulu la Yehova? Mawu a Yehova amatilimbikitsa kuti tizimvera amene akutsogolera komanso tiziwagonjera. (Deut. 30:16; Aheb. 13:7, 17) Mtima wopezera ena zifukwa komanso wosafuna kuuzidwa zochita sufunika m’gulu la Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti mtimawu ungachititse kuti mumpingo musakhalenso mtendere, mgwirizano komanso chikondi. M’bale wokhulupirika sangafune kukhala ndi mtima wopanda ulemu komanso wosakhulupirika ngati wa Diotirefe. (3 Yoh. 9, 10) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi ineyo ndimalimbikitsa abale ndi alongo kuti akhale okhulupirika kwa Yehova? Nanga kodi ndimatsatira mwamsanga malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa? w16.11 2:10, 11
Lachisanu, July 20
Mzinda umene ndakuchititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunira mtendere.—Yer. 29:7.
Ayuda amene anamvera zimene Yehova anawauzazi, ankakhala bwinobwino ku Babuloko. Ababulo ankawalola kuti aziyenda mwaufulu komanso kuti azichita okha zinthu zina. Mumzinda wa Babulo munkachitika malonda osiyanasiyana. Ndipo zimene anthu ofukula zinthu zakale anapeza zimasonyeza kuti Ayuda ambiri anaphunzira ntchito zamanja komanso kuchita bizinezi ndipo ena analemera. Choncho Ayudawa ankakhala bwino ku Babulo kusiyana ndi mmene Aisiraeli ankakhalira ku Iguputo pamene anali akapolo. (Eks. 2:23-25) Kodi zikanatheka kuti Aisiraeli adzalambirenso Mulungu bwinobwino? Pa nthawiyo zinkaoneka ngati zosatheka. Tikutero chifukwa chakuti malamulo a Ababulo sankalola kumasula akapolo. Iye anali atalonjeza anthu akewo kuti adzawamasula ku ukapolo. Zimenezi sizikanalephereka chifukwa Mawu a Mulungu amakwaniritsidwa.—Yes. 55:11. w16.11 4:3, 5
Loweruka, July 21
Tinafa ku uchimo.—Aroma 6:2.
Popeza Paulo ndi Akhristu enawo anali adakali moyo, kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti iwo ‘anafa ku uchimo?’ Mulungu anagwiritsa ntchito dipo kuti athandize Paulo komanso a Akhristu a nthawi yake. Iye anawakhululukira machimo awo ndipo anawadzoza ndi mzimu wake woyera kuti akhale ana ake. Ankafuna kuti akakhalabe okhulupirika, adzalamulire ndi Khristu. Ndiyeno Paulo anayerekezera moyo wawo ndi wa Yesu pofuna kusonyeza kuti Akhristuwo anasintha kwambiri. Anati Yesu atafa, anaukitsidwa ndi thupi loti silingafe. N’chifukwa chake Baibulo limati, “imfa sikuchitanso ufumu pa iye.” Mofanana ndi zimenezi, Akhristuwo anafa pamene anasiya moyo wauchimo. Iwo sankalolanso kuti azichita zinthu motsatira zilakolako zoipa. Koma ankayesetsa kukhala ndi moyo wosangalatsa Mulungu. Choncho tingati ‘anafa ku uchimo koma anali amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.’—Aroma 6:9, 11. w16.12 1:9, 10
Lamlungu, July 22
Kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.—Aroma 8:6.
Kuika maganizo pa zinthu za mzimu sikutanthauza kuti munthu azingokhalira kuchita zinthu zokhudza kulambira. Sizitanthauzanso kuti munthu azingolankhula ndi kuganiza zokhudza Baibulo, Yehova ndi dziko latsopano basi. Tizikumbukira kuti Paulo ndi Akhristu ena okhulupirika ankachitanso zinthu zina. Iwo ankadya komanso kumwa. Ndipo ambiri anali ndi mabanja komanso ankagwira ntchito. (Maliko 6:3; 1 Ates. 2:9) Komabe Paulo ndi Akhristu enawo sanalole kuti zinthu za tsiku ndi tsiku zikhale zofunika kwambiri pa moyo wawo. Mwachitsanzo, tikudziwa kuti Paulo ankagwira ntchito yopanga matenti. Koma Baibulo limasonyeza kuti iye ankaona kuti chofunika kwambiri ndi ntchito yolalikira ndiponso kuphunzitsa. Choncho iye ankatanganidwa kwambiri kugwira ntchitoyi ndipo analimbikitsanso Akhristu a ku Roma kuti azichita zomwezo. (Mac. 18:2-4; 20:20, 21, 34, 35) Paulo ankaona kuti kutumikira Mulungu n’kofunika kwambiri ndipo Akhristu a ku Roma ankafunika kumutsanzira. Ifenso masiku ano tiyenera kuchita chimodzimodzi.—Aroma 15:15, 16. w16.12 2:5, 15, 16
Lolemba, July 23
Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.—Miy. 19:17.
Yehova amayamikira kwambiri zonse zimene timachita pomutumikira. Amadziwanso zinthu zimene zimatichititsa kudzikayikira kapena kuchita mantha. Iye amatimvera chisoni tikakhala ndi nkhawa chifukwa cha mavuto azachuma. Amatimvetsanso tikamalephera kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha matenda kapena mavuto ena. Choncho tisamakayikire mfundo yoti Yehova amayamikira kwambiri zimene atumiki ake amachita kuti akhalebe okhulupirika. (Aheb. 6:10, 11) Baibulo limati Yehova ndi “Wakumva pemphero” choncho tisamakayikire zoti adzayankha mapemphero athu. (Sal. 65:2) Iye ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akor. 1:3) Akhoza kutilimbikitsa pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu. Yehova amasangalala kwambiri nafenso tikamachitira chifundo anzathu. (Mat. 6:3, 4) Choncho tikathandiza munthu amene ali pa mavuto, Yehova amaona kuti tamukongoza iyeyo ndipo amalonjeza kuti adzatibwezera. w16.12 4:13, 14
Lachiwiri, July 24
Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.—2 Akor. 3:17.
Yesu ali padzikoli, anagwiritsa ntchito bwino ufulu wake wosankha zochita ndipo anakana mayesero a Satana. (Mat. 4:10) Komanso atatsala pang’ono kuperekedwa, iye anapemphera kwa Atate wake ndipo anasonyeza kuti ankafunitsitsa kukhalabe wokhulupirika. Anati: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu chifuniro chanu chichitike, osati changa.” (Luka 22:42) Tiyeni tizitsanzira Yesu ndipo nafenso tizigwiritsa ntchito bwino ufulu wathu wosankha, pochita chifuniro cha Yehova. Koma kodi n’zothekadi kuchita zimenezi? Inde n’zotheka, popeza nafenso tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu. (Gen. 1:26) Komabe kwa ifeyo, kukhala ndi ufulu wosankha sikukutanthauza kuti tingathe kumangochita chilichonse. Paja Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wochita chilichonse. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti pali zinthu zina zimene sitiyenera kuchita ndipo tiyenera kutsatira zimene Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, akazi ayenera kugonjera amuna awo ndipo ana ayenera kumvera makolo.—Aef. 5:22; 6:1. w17.01 2:4, 5
Lachitatu, July 25
Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.—Aroma 12:3.
Masiku ano mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikukula ndipo izi n’zosangalatsa kwambiri. Koma zimenezi zikupangitsa kuti pazifunika kusintha zinthu zina m’gululi. Choncho kusintha kukatikhudza ifeyo tiyenera kukhala odzichepetsa. Tiziganizira kwambiri zimene Yehova akufuna osati zofuna zathu. Tikatero tidzakhala ogwirizana. Paulo analembera Akhristu a ku Roma kuti: “Monga tilili ndi ziwalo zambiri m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu.” (Aroma 12:4, 5) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tiyeni tizichita zimene tingathe potumikira Yehova. Ngati ndinu wachikulire, yesetsani kuphunzitsa achinyamata ntchito zanu. Nanunso achinyamata muyenera kuvomera mukapatsidwa udindo ndipo muzikhala odzichepetsa komanso muzilemekeza achikulire. Akazi nawonso ayenera kutsanzira Purisikila amene ankathandiza mwamuna wake mokhulupirika ngakhale kuti zinthu zinkasintha pa moyo wawo.—Mac. 18:2. w17.01 5:15, 16
Lachinayi, July 26
M’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambiri ndine.—Ower. 6:15.
Gidiyoni anavomereza modzichepetsa kuti anali munthu wamba. Yehova atamupatsa ntchito yoti achite, iye anaonetsetsa kuti wamvetsa zoyenera kuchita ndipo anadalira Yehova kuti amutsogolere. (Ower. 6:36-40) Gidiyoni anali wolimba mtima. Komabe ankachita zinthu mosamala. (Ower. 6:11, 27) Komanso iye sanagwiritse ntchito udindo wake kuti atchuke. M’malomwake atangomaliza ntchito imene Yehova anamupatsa, anabwerera kwawo. (Ower. 8:22, 23, 29) Kukhala odzichepetsa sikutanthauza kuti tisamayesetse kuti tiyenerere udindo kapena tizikana udindo popanda chifukwa. Paja Malemba amatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kupita patsogolo. (1 Tim. 4:13-15) Koma kodi nthawi zonse timafunika kupatsidwa utumiki wina kuti zioneke kuti tikupita patsogolo? Ayi. Yehova angatidalitse ndipo tingathe kumapita patsogolo ngakhale kuti sitinasinthe utumiki. Tingathenso kumasonyeza kwambiri makhalidwe abwino. w17.01 3:15, 16
Lachisanu, July 27
[Mulungu] anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.—1 Yoh. 4:9.
Yehova analolera kupereka Mwana wake wamtengo wapatali kuti akhale dipo. (1 Pet. 1:19) Iye amakonda kwambiri anthu moti analolera kuti Mwana wakeyu afe chifukwa chofuna kuwapulumutsa. Apa tingati Yesu anatenga udindo wokhala bambo athu umene Adamu anataya. (1 Akor. 15:45) Zimene Yesu anachitazi zimathandiza kuti tidzapeze moyo wosatha komanso kuti tidzabwerere m’banja la Mulungu. Yehova amagwiritsa ntchito dipoli kuti alandirenso anthu m’banja lake popanda kuphwanya mfundo zake zachilungamo. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri anthu onse okhulupirika akadzakhalanso angwiro. Pa nthawiyo, mbali yakumwamba ya banja la Mulungu idzakhala yogwirizana kwambiri ndi mbali yapadziko lapansi. Mwachidule tingati tonsefe tidzakhala ana enieni a Mulungu. (Aroma 8:21) Mtima woyamikira uyenera kutilimbikitsa kuthandiza anthu kudziwa kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene ingawathandize. w17.02 1:17, 19
Loweruka, July 28
Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?—Mat. 24:45.
Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013 inanena kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi kagulu ka abale odzozedwa amene ali m’Bungwe Lolamulira. Bungwe Lolamulira limasankha zochita mogwirizana. N’chifukwa chiyani tikutero? Abale a m’Bungweli amakumana mlungu uliwonse ndipo zimenezi zimathandiza kuti azikambirana momasuka komanso azigwirizana. (Miy. 20:18) Chaka chilichonse amasintha tcheyamani wa misonkhano yawo ndipo amachita zimenezi chifukwa choti amaona kuti palibe munthu wa m’Bungweli amene amaposa mnzake. (1 Pet. 5:1) Bungweli lili ndi makomiti 6 ndipo tcheyamani wa komiti iliyonse amasinthanso chaka chilichonse. Munthu aliyense amene ali m’Bungwe Lolamulira sadziona ngati mtsogoleri wa abale ake koma ngati ‘wantchito wapakhomo’ amene amadyetsedwa ndi kapolo wokhulupirika ndipo amamvera kapoloyo. Koma sikuti Bungwe Lolamulira silingalakwitse zinthu pa nkhani yophunzitsa komanso kayendetsedwe ka gulu. w17.02 4:10-12
Lamlungu, July 29
[Mulungu] amene sanaumire ngakhale Mwana wake koma anamupereka m’malo mwa ife tonse.—Aroma 8:32.
Tingasonyeze kuti timayamikira dipo podzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa. Tikabatizidwa timasonyeza kuti “ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Yehova amachita zinthu zonse chifukwa cha chikondi ndipo amafuna kuti aliyense amene amamulambira azisonyeza chikondicho. (1 Yoh. 4:8-11) Ndiyeno tikamakonda anzathu timasonyeza kuti tikufuna kukhala ‘ana a Atate wathu wakumwamba.’ (Mat. 5:43-48) Paja lamulo lalikulu kwambiri ndi loti tizikonda Yehova ndipo lachiwiri lake ndi lakuti tizikonda anzathu. (Mat. 22:37-40) Tikamamvera lamulo loti tizilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, timasonyeza kuti timakonda anzathu ndipo timalemekeza Mulungu. Tikamachita zimenezi, chikondi chathu kwa Mulungu “chimakhala chokwanira.”—1 Yoh. 4:12, 20. w17.02 2:13, 14
Lolemba, July 30
Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni, koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatirani ameneyo.—1 Maf. 18:21.
Ena angaganize kuti zinalinso zosavuta kusankha pa nkhaniyi chifukwa woyenera kumulambira ndi Yehova. Munthu woganiza bwino sangasankhe kulambira mulungu wopanda moyo. Koma Aisiraeliwo analephera kusankha ndipo ‘ankangokayikakayika.’ Choncho Eliya anawalimbikitsa kuti ayenera kusankha kulambira Yehova chifukwa ndi Mulungu woona. N’chifukwa chiyani Aisiraeliwa zinkawavuta kusankha mwanzeru pa nkhaniyi? Choyamba, anali atasiya kukhulupirira Yehova ndipo sankamumveranso. Iwo sankadziwa zolondola, sankadalira Mulungu komanso sankatsogoleredwa ndi nzeru zake. Akanakhala kuti ankadziwa zolondola za Mulungu ndipo ankachita zinthu mogwirizana ndi zomwe ankadziwazo, akanatha kusankha mwanzeru. (Sal. 25:12) Chachiwiri, ankalola kuti azingoyendera maganizo a anthu osalambira Yehova, mwinanso mpaka kumawalola kuti aziwasankhira zochita. Aisiraeli anasokonezeka kwambiri ndi anthuwa moti anayamba kulambira mafano. Ndipotu Yehova anali ataneneratu kuti zoterezi zidzachitika.—Eks. 23:2. w17.03 2:6, 7
Lachiwiri, July 31
[Hezekiya] anaphwanyaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga.—2 Maf. 18:4.
Mukaganizira chitsanzo cha Hezekiya, kodi mukuona kuti pali chilichonse chimene chikusokoneza ubwenzi wanu ndi Mulungu? Nanga pali zimene zikukulepheretsani kuti muzimulambira mokhulupirika? Mwachitsanzo, ambiri m’dzikoli amachita zinthu ngati amalambira anthu. Amagomera anthu otchuka komanso ena amene sawadziwa n’komwe. Ena amatha nthawi yambiri pamalo ochezera pa intaneti n’kumawerenga za anthu amenewo, kuona zithunzi zawo komanso kulemberana nawo mameseji. N’zoona kuti tingagwiritse ntchito intaneti polumikizana ndi achibale komanso anzathu. Koma kupanda kusamala tikhoza kumawononga nthawi yambiri pa zinthu ngati zimenezi. Vuto linanso ndi loti tingayambe kunyada ngati anthu ambiri asonyeza kuti akukonda zithunzi kapena zinthu zina zimene taika. Apo ayi tikaona kuti sakulembanso zosonyeza kuti aona zimene taika, tingakhumudwe. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapewa kulambira anthu? Nanga ndimapewa kuwononga nthawi yambiri pa zinthu zosafunika kwenikweni?’—Aef. 5:15, 16. w17.03 3:14, 17