August
Lachitatu, August 1
Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.—Yak. 1:4.
Nkhondo inali itafika poipa kwambiri. Asilikali achiisiraeli omwe ankatsogoleredwa ndi Gidiyoni anathamangitsa adani awowo usiku wonse kwa mtunda wamakilomita pafupifupi 32. Aisiraeli ankadziwa kuti iyi sinali nthawi yoti asiye kumenya nkhondo. Choncho, anapitirizabe ‘kuthamangitsa’ a Midiyani mpaka kuwagonjetsa. (Ower. 7:22; 8:4, 10, 28) Masiku anonso tikumenya nkhondo yovuta. Tikulimbana ndi Satana, dziko loipali komanso matupi athu ochimwawa. Ambirife tamenya nkhondoyi kwa zaka zambiri ndipo Yehova wakhala akutithandiza. Komabe nthawi zina tingaone kuti tatopa kumenyana ndi adani athu ndiponso kuyembekezera mapeto a dzikoli. Komatu nkhondoyi idakalipo. Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza ano tidzakumana ndi mayesero ndi mavuto ambiri. Koma ananenanso kuti tikhoza kupambana ngati titapirira.—Luka 21:19. w16.04 2:1, 2
Lachinayi, August 2
Anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.—Mac. 2:42.
Tikakhala pamisonkhano, Mlangizi wathu wamkulu amatitsogolera pogwira ntchito Mawu ake. (Yes. 30:20, 21) Ngakhale anthu ena akafika pamisonkhano yathu amadziwa kuti ‘Mulungu ali pakati pathu.’ (1 Akor. 14:23-25) Zimene timaphunzira zimachokera kwa Yehova ndipo amatitsogolera ndi mzimu woyera. Tikakhala pamisonkhano timaona kuti Yehova amatikonda ndiponso amatisamalira. Choncho misonkhano imatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Yesu anati: “Kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndidzakhala pakati pawo.” (Mat. 18:20) Baibulo limati Khristu ndi Mutu wampingo ndipo amayenda pakati pa mipingo. (Chiv. 1:20–2:1) Izi zikusonyeza kuti Yehova ndi Yesu amakhala nafe pamisonkhano ndipo amatilimbikitsa. Yehova amasangalala akaona kuti tikuyesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Mwana wake komanso iyeyo. w16.04 3:13, 14
Lachisanu, August 3
Usamafulumire kukwiya mumtima mwako.—Mlal. 7:9.
Pamene abale ndi alongo ena anali pakaphwando, mlongo wina anapereka moni kwa abale ena awiri. Kenako m’bale winayo anauza mnzakeyo kuti sanasangalale ndi zimene mlongo uja anachita popereka moniyo. Komabe mnzakeyo anam’kumbutsa zoti mlongoyo wakhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka 40 ndipo ayenera kuti analibe cholinga chomukhumudwitsa. Atakambirana kwakanthawi, m’baleyu anavomereza kuti mnzakeyo akunenadi zoona. Choncho anaona kuti ndi bwino angoinyalanyaza nkhaniyo. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzochi? Anthu ena akachita kapena kulankhula zotikhumudwitsa, tingasankhe kungozinyalanyaza. Munthu wachikondi amakhululuka anthu ena akamulakwira. (Miy. 10:12; 1 Pet. 4:8) Yehova amaona kuti munthu amene ‘amanyalanyaza cholakwa’ ndi “wokongola.” (Miy. 19:11) Choncho munthu akakulakwirani muzidzifunsa kuti, ‘Kodi n’zotheka kungoinyalanyaza nkhaniyi, kapena pakufunika kuti tikambirane?’ w16.05 1:8, 9
Loweruka, August 4
Mulungu amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.
Kodi ndi ndani akulalikira uthenga wabwino masiku ano? Mosakayikira, tingayankhe kuti ndi “Mboni za Yehova.” Tikutero chifukwa chakuti timalalikira uthenga woyenera womwe ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Komanso timagwiritsa ntchito njira yoyenera chifukwa timapita kwa anthuwo. Timagwira ntchito yolalikirayi chifukwa timakonda Yehova ndi anthu osati chifukwa chofuna kupeza ndalama. Ndipotu timalalikira padziko lonse kwa anthu amitundu yonse komanso m’zilankhulo zonse. Tipitirizabe kugwira ntchito yolalikirayi mwakhama mpaka mapeto afike. Timachita chidwi tikaona zimene tikukwaniritsa kuchita pa ntchito yolalikira. Koma kodi n’chiyani chimatithandiza kukwaniritsa zonsezi? Mawu amulemba la leroli amene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Filipi, akuyankha funso limeneli. Tiyeni tonsefe tizidalira Atate wathu wachikondi kuti azitithandiza pamene tikuyesetsa kukwaniritsa utumiki wathu.—2 Tim. 4:5. w16.05 2:17, 18
Lamlungu, August 5
Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.—Aroma 12:9.
Tikasankha kutumikira Yehova n’kumayesetsa kuchita zimene amafuna, timasonyeza kuti timamukonda ndipo timafunitsitsa kumusangalatsa. Timasonyezanso kuti timafuna kuti azitilamulira. Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira. Choncho Yehova amayamikira tikamamumvera mwa kufuna kwathu chifukwa timasonyeza kuti tili kumbali yake. (Yobu 2:3-5; Miy. 27:11) Koma akanapanda kulola kuti tizichita khama posintha makhalidwe oipa, sizikanadziwika kuti timasankha tokha kukhala kumbali yake. Yehova amatiuza kuti ‘tiziyesetsa mwakhama’ kutsanzira makhalidwe ake. (2 Pet. 1:5-7; Akol. 3:12) Amafunanso kuti tizichita khama kulamulira maganizo ndi mtima wathu. (Aroma 8:5) Tikakwanitsa kuchita zimenezi timasangalala chifukwa timadziwa kuti Baibulo likusinthabe moyo wathu. w16.05 4:12, 13
Lolemba, August 6
Yehova, . . . inu ndinu Wotiumba.—Yes. 64:8.
Yehova akamafuna kuumba munthu amadziwa kuti munthuyo ndi wotani ndipo amamuumba mogwirizana ndi mmene alili. (Sal. 103:10-14) Amaumba munthu aliyense payekha ndipo amaganizira zimene munthuyo sangakwanitse, zimene amalakwitsa komanso mmene amachitira pa zinthu zauzimu. Zimene Mwana wake ankachita ali padziko lapansi zimasonyeza mmene Yehova amationera anthufe. Taganizirani zimene Yesu ankachita atumwi ake akamakangana kuti wamkulu ndani. Mukanakhala kuti munalipo, kodi mukanaganiza chiyani? Mwina mukanaona kuti atumwiwo ndi odzikuza ndipo sangaumbike. Komatu Yesu sanawaone choncho. Anadziwa kuti angathe kuumbika. Ankangofunika kuwakomera mtima, kuwapatsa malangizo komanso kuwasonyeza chitsanzo cha kudzichepetsa. (Maliko 9:33-37; 10:37, 41-45; Luka 22:24-27) Yesu ataukitsidwa atumwiwo analandira mzimu woyera ndipo unawathandiza kuti asamaganizire kwambiri za udindo kapena kutchuka koma za ntchito imene anawapatsa.—Mac. 5:42. w16.06 1:10
Lachiwiri, August 7
Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.—Deut. 6:4.
Palibenso mulungu wina amene angafanane ndi Yehova. (2 Sam. 7:22) Choncho Mose anakumbutsa Aisiraeli kuti sankayenera kutsanzira anthu a mitundu ina amene ankalambira milungu yosiyanasiyana. Anthuwa ankakhulupirira kuti milungu yawoyo imayang’anira zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Aiguputo ankalambira mulungu wadzuwa wotchedwa Ra komanso mulungu wa mitambo wotchedwa Nut. Analinso ndi mulungu wadziko dzina lake Geb komanso wa mtsinje wa Nailo wotchedwa Hapi. Iwo ankalambiranso nyama zosiyanasiyana. Yambiri mwa milunguyi, Yehova anaichititsa manyazi pamene anagwetsera Aiguputo miliri 10. Mulungu wotchuka wa Akanani anali Baala. Ameneyu anali mulungu wobereketsa, wa mitambo, wa mvula komanso wa mphepo. M’madera enanso anthu ankakhulupirira kuti Baala amawateteza. (Num. 25:3) Koma Aisiraeli anayenera kukumbukira kuti Mulungu wawo ndi “Yehova mmodzi.”—Deut. 4:35, 39. w16.06 3:4, 5
Lachitatu, August 8
[Muziwaphunzitsa] kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.—Mat. 28:20.
Chitsanzo cha Yesu chikutiphunzitsa kuti nafenso tiyenera kukhulupirira Yehova komanso anthu ake. Ndipotu tikaona zimene Yehova akuchita kudzera mwa atumiki ake masiku otsiriza ano, timasowa chonena. Mwachitsanzo, ndife ogwirizana ndipo tikukwanitsa kulalikira padziko lonse. Koma anthu ena satha kuchita zimenezi chifukwa alibe mzimu wa Yehova. Lemba la Yesaya 65:14 limafotokoza mmene zinthu zilili pakati pa anthu a Mulungu. Limati: “Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” Anthu a Yehovafe timasangalala kwambiri chifukwa Yehova amatitsogolera komanso amatithandiza kuchita zinthu zabwino zambiri. Koma anthu a m’dziko la Satanali sizikuwayendera bwino chifukwa zinthu zikungoipiraipira. Tiyeni tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova n’kumatsatira malangizo ake. w16.06 4:10-12
Lachinayi, August 9
Khalanibe maso.—Mat. 25:13.
Tikhoza kuphunzira zambiri pa nkhani yokhudza kukhala maso tikaganizira zimene alonda a m’mizinda yakale ankachita. Kalelo mizinda yaikulu monga Yerusalemu inkakhala ndi mipanda italiitali. Mipanda imeneyi inkawateteza ndipo inkathandiza kuti alonda aziona ngati adani akubwera. Alondawo ankakhala pampanda kapena pageti usana ndi usiku. Kukamabwera choopsa chilichonse, iwo ankayenera kudziwitsa anthu amumzindawo. (Yes. 62:6) Alondawa ankadziwa kuti ayenera kukhala maso nthawi zonse kuti adziwe zimene zikuchitika chifukwa kupanda kutero, akanaphetsa anthu ambiri amumzindawo. (Ezek. 33:6) Wolemba mbiri wina dzina lake Josephus ananena kuti, Aroma analowa mumzinda wa Yerusalemu mu 70 C.E. chifukwa chakuti alonda apageti anagona. Aromawo anapita kukayatsa kachisi kenako n’kuwononga mzinda wonsewo. Chimenechi chinali chimake cha mavuto oopsa amene anachitika ku Yerusalemu. w16.07 2:2, 7, 8
Lachisanu, August 10
Chenjerani kuti musasochere pokopeka ndi zolakwa za anthu ophwanya malamulowo, kuopera kuti mungalephere kukhala olimba ndipo mungagwe.—2 Pet. 3:17.
Timapeza madalitso ambiri chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu. Koma sitiyenera kugwiritsa ntchito molakwika kukoma mtima kumeneku. Kalelo panali Akhristu ena amene ankafuna kutenga “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lotayirira.” (Yuda 4) Iwo ankaganiza kuti akhoza kumachimwa dala kenako n’kupempha Yehova kuti awakhululukire. Chomvetsa chisoni kwambiri n’chakuti ankakopa Akhristu ena kuti azichitanso zomwezo. Masiku anonso, aliyense wochita zimenezi amanyoza “mzimu wa Mulungu, yemwe amasonyeza kukoma mtima kwakukulu.” (Aheb. 10:29) Koma pali Akhristu ena amene asocheretsedwa ndi Satana n’kumaganiza kuti akhoza kumangochimwa ndipo Yehova aziwakhululukira. N’zoona kuti Yehova amatikhululukira tikalapa koma amafunanso kuti tizichita khama polimbana ndi mtima wofuna kuchimwa. w16.07 3:16, 17
Loweruka, August 11
Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.—Mat. 19:9.
Munthu akathetsa banja pa zifukwa zina, osati chigololo, sakhala womasuka kuti akwatiranenso ndi wina. Mkhristu angasankhe kukhululukira amene wachita chigololo n’kulapa ngati mmene Hoseya anakhululukira Gomeri. Nayenso Yehova anakhululukira mtundu wa Isiraeli umene tingati unachita chigololo. (Hos. 3:1-5) Mfundo ina yoyenera kuikumbukira ndi yakuti, ngati mwamuna kapena mkazi wachita chigololo ndiyeno mnzakeyo wavomera kugona naye, ndiye kuti wamukhululukira ndipo palibenso chifukwa cha m’Malemba chothetsera banjalo. Yesu atanena mawu amulemba la leroli, ananenanso za anthu amene “ali ndi mphatso” yosakhala pa banja. Ndiyeno ananena kuti: “Amene angathe kuchita zimenezi achite.” (Mat. 19:10-12) Pali anthu ambiri amene asankha kusakhala pa banja n’cholinga choti azitumikira Yehova popanda zododometsa. Anthu oterewa amafunika kuwayamikira kwambiri. w16.08 1:15, 16
Lamlungu, August 12
Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye. . . . Onse omuopa sasowa kanthu.—Sal. 34:8, 9.
Achinyamata ali ndi mphamvu ndipo angathe kuchita zambiri potumikira Yehova. (Miy. 20:29) Achinyamata ena amene akutumikira pa Beteli amagwira ntchito yosindikiza ndi kukonza Mabaibulo komanso mabuku athu. Pamene enanso amathandiza pa ntchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu. Pakachitika ngozi zadzidzidzi, achinyamata ena amathandizana ndi abale ndi alongo aluso pogwira ntchito yothandiza anthu amene akuvutika. Ndiponso apainiya ambiri achinyamata amadzipereka kuphunzira zilankhulo zina n’kumalalikira anthu a zilankhulozo. Wamasalimo anaimba kuti: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.” (Sal. 34:10) Yehova sagwiritsa mwala anthu amene amamutumikira mwakhama. Tikamayesetsa kuchita zonse zimene tingathe, timakhala ngati ‘tikulawa n’kuona kuti iye ndi wabwino.’ Kunena zoona, tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse timasangalala kwambiri. w16.08 3:5, 8
Lolemba, August 13
Ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala dalitso. Musachite mantha. Limbani mtima ndipo mukonzeke kugwira ntchito.—Zek. 8:13.
Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera. (1 Mbiri 29:12) Choncho m’pofunika kuti tizipempha mzimuwu chifukwa ndi umene ungatithandize kulimbana ndi mavuto omwe Satana angatibweretsere. (Sal. 18:39; 1 Akor. 10:13) Tilinso ndi mwayi chifukwa tili ndi Mawu a Mulungu omwe anthu analemba mothandizidwa ndi mzimu woyera. Taganiziraninso za chakudya chauzimu chochokera m’Baibulo chimene timalandira mwezi uliwonse. Mawu a pa Zekariya 8:9, 13 analankhulidwa pa nthawi imene kachisi wa ku Yerusalemu ankamangidwanso ndipo ndi othandizanso masiku ano. Mulungu amatipatsanso mphamvu pogwiritsa ntchito zimene timaphunzira pa misonkhano yampingo, yadera, yachigawo komanso masukulu osiyanasiyana. Zimene timaphunzirazi zimatithandiza kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu. Zimatithandizanso kukhala ndi zolinga zauzimu komanso kuti tizitha kukwaniritsa maudindo athu. (Sal. 119:32) Kodi nanunso mumayesetsa kuti muzipeza mphamvu kuchokera pa zimene timaphunzira? w16.09 1:10, 11
Lachiwiri, August 14
Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.—Aroma 12:2.
Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chinkasonyeza kuti Yehova sasangalala ndi zovala zimene anthu akavala, pamakhala povuta kusiyanitsa ngati munthuyo ndi wamkazi kapena wamwamuna. (Deut. 22:5) Malangizo amene Mulungu anapereka okhudza kavalidwe amasonyeza kuti iye sasangalalanso ndi masitayilo a zovala amene amapangitsa kuti amuna azioneka ngati akazi, akazi azioneka ngati amuna, kapena anthu asamathe kusiyanitsa pakati pa amuna ndi akazi. M’Baibulo muli mfundo zimene zingathandize Akhristu kuti azisankha bwino pa nkhani ya zovala. Mfundo zimenezi zimagwira ntchito mosatengera kumene munthu amakhala, chikhalidwe chake kapena nyengo ya kwawoko. Sitifunika mndandanda wa malamulo onena za zovala zoyenera ndi zosayenera. M’malomwake timatsatira mfundo za m’Malemba ndipo Mkhristu aliyense amasankha zimene angakonde, koma mogwirizana ndi mfundozo. w16.09 3:3, 4
Lachitatu, August 15
Pamenepo ophunzira ake onse anathawa ndi kumusiya yekha.—Maliko 14:50.
Olemba Baibulo anali olimba mtima komanso achilungamo. Kuganizira mfundo imeneyi kumalimbitsanso chikhulupiriro chathu. Tikutero chifukwa chakuti olemba mbiri akale ankalemba zotamanda dziko lawo ndi atsogoleri awo. Koma aneneri a Yehova ankanena zinthu zoona nthawi zonse. Iwo ankalemba zolakwa zimene anthu awo kapena mafumu awo ankachita. (2 Mbiri 16:9, 10; 24:18-22) Ankafotokozanso zimene iwowo komanso atumiki ena a Mulungu analakwitsa. (2 Sam. 12:1-14) Ambiri amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu akaona mmene mfundo zake zimathandizira anthu. (Sal. 19:7-11) Mfundo za M’Baibulo zimatiteteza kuti tipewe miyambo ya zipembedzo zonyenga komanso kukhulupirira zamizimu. (Sal. 115:3-8) Anthu amene amakhulupirira zoti kulibe Mlengi amaona kuti zinthu zam’chilengedwe zili ngati milungu yawo. Anthuwo amaganizanso kuti tsogolo lawo lonse lili m’manja mwawo. Koma vuto ndi lakuti sapereka chiyembekezo chilichonse choti angasinthe zinthu m’dzikoli.—Sal. 146:3, 4. w16.09 4:10, 11
Lachinayi, August 16
Muloleni akunkhe . . . , ndipo musam’vutitse.—Rute 2:15.
Zimene Boazi anauza Rute zikusonyeza kuti ankaganizira mavuto amene ankakumana nawo chifukwa chokhala m’dziko lachilendo. Iye anamuuza kuti azikhala limodzi ndi atsikana ake antchito n’cholinga choti asavutitsidwe ndi aliyense. Anamuuzanso kuti azidya nawo chakudya komanso kumwa madzi. Iye ankamulankhula mwaulemu komanso anamulimbikitsa. (Rute 2:8-10, 13, 14) Boazi anachita chidwi atadziwa kuti Rute anakomera mtima Naomi komanso anayamba kulambira Yehova. Apa zinali ngati Rute wathawira ‘m’mapiko a Yehova’ ndipo Yehovayo anagwiritsa ntchito Boazi pofuna kuti amuthandize. (Rute 2:12, 20; Miy. 19:17) Nafenso tikamakomera mtima anthu a mtundu uliwonse, timawathandiza kuzindikira kuti Yehova amawakonda.—1 Tim. 2:3, 4. w16.10 1:10-12
Lachisanu, August 17
Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha, pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa.—Sal. 34:4.
Nafenso tiyenera kupemphera kuchokera mumtima. Tisamakayikire zoti adzatiyankha komanso kutithandiza kuti tizisangalala ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. Ndipo tikazindikira kuti Yehova watiyankha, chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri. (1 Yoh. 5:14, 15) Koma tizikumbukiranso kuti mzimu wa Mulungu ndi umene umatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro. Choncho tiyeni tizitsatira malangizo a Yesu oti tipitirize kupempha Mulungu kuti azitipatsa mzimu wake. (Luka 11:9, 13) Koma si bwino kumangopemphera kwa Yehova tikafuna thandizo. Tiyeneranso kumuyamika komanso kumutamanda chifukwa cha zinthu zimene wachita. (Sal. 40:5) Mapemphero athu ayenera kusonyeza kuti timaganiziranso ‘amene ali m’ndende ngati kuti tamangidwa nawo limodzi.’ Tiyeneranso kupempherera abale athu padziko lonse makamaka amene ‘akutitsogolera.’ Ndipotu timayamikira kwambiri tikaona kuti Yehova wayankha mapemphero athu.—Aheb. 13:3, 7. w16.10 3:8, 9
Loweruka, August 18
Mwapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro, osati mwa inu nokha, koma monga mphatso ya Mulungu.—Aef. 2:8.
Masiku ano anthu a Yehova oposa 8 miliyoni amasonyeza kuti amakhulupirira zoti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira. Izi zachititsa kuti akhale m’paradaiso wauzimu ndipo amayesetsa kusonyeza makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Zimenezi zikusonyeza kuti kukhala ndi chikhulupiriro komanso chikondi kumathandiza kwambiri. Zonsezi zikutheka chifukwa choti Mulungu amatithandiza. Tingati izi ‘zatchukitsa Yehova, ndipo zidzakhala chizindikiro choti sichidzachotsedwa mpaka kalekale.’ (Yes. 55:13) Paradaiso wathu wauzimu apitirizabe mpaka padziko lonseli padzakhale anthu angwiro, olungama ndi osangalala n’kumatamanda dzina la Yehova mpaka kalekale. Choncho tiyeni tipitirize kusonyeza kuti timakhulupirira malonjezo a Yehova. w16.10 4:18, 19
Lamlungu, August 19
Ena akuyenda mosalongosoka pakati panu.—2 Ates. 3:11.
Ndi bwino kutsatira malangizo ochokera m’Malemba amene akulu amatipatsa. Chitsanzo ndi malangizo amene Paulo anapereka kumpingo wa Atesalonika okhudza anthu oyenda mosalongosoka. Pa nthawiyo anthu ena ‘sankagwira ntchito koma ankangokonda kulowerera nkhani zosawakhudza.’ Akulu anawapatsa malangizo koma anthuwo sanamvere. Ndiyeno Paulo anauza mpingowo kuti anthu oterowo ndi ofunika ‘kuwaika chizindikiro n’kusiya kuchitira nawo zinthu limodzi.’ Komabe apa Paulo sankatanthauza kuti aziwaona ngati adani awo. (2 Ates. 3:11-15) Masiku ano, akulu angakambe nkhani yochenjeza anthu za munthu wina mumpingo amene akupitirizabe kuchita khalidwe loipa, monga kuchita chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira. (1 Akor. 7:39) Kodi inuyo mumatani ngati mwadziwa munthu amene wachita zimene zikunenedwazo? Kodi mumasiyadi kuchita naye zinthu zina? Zimenezi zingamuthandize kuti azindikire kulakwa kwake n’kusintha. w16.11 2:13
Lolemba, August 20
Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.—Mac. 20:30.
Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Ayuda ambiri komanso anthu omwe sanali Ayuda anadzozedwa ndi mzimu woyera. Akhristu atsopanowa anakhala “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera.” (1 Pet. 2:9, 10) Atumwi ndi amene ankatsogolera mipingo. Koma atumwi onse atamwalira anthu ena anayamba kulankhula “zinthu zopotoka” n’cholinga choti “apatutse ophunzira aziwatsatira.” (2 Ates. 2:6-8) Ambiri mwa anthuwa anali ndi maudindo mumpingo ndipo kenako anadzakhala “mabishopu.” Apa m’pamene panayambira magulu a atsogoleri achipembedzo ngakhale kuti Yesu anali atauza otsatira ake kuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mat. 23:8) Koma anthuwa ankakonda nzeru za Aristotle ndi Plato ndipo ankaphunzitsa zinthu zabodza. Patapita nthawi, izi zinachititsa kuti anthu asamaphunzirenso mfundo zolondola za m’Mawu a Mulungu. w16.11 4:8
Lachiwiri, August 21
Musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo.—Aroma 6:12.
Tisanakhale Akhristu tinkachita machimo ambiri. Mwinanso sitinkazindikira n’komwe kuti zimene tikuchitazo n’zoipa pamaso pa Mulungu. Tinali “akapolo a zonyansa ndiponso akapolo a kusamvera malamulo.” Choncho tinali “akapolo a uchimo.” (Aroma 6:19, 20) Koma titaphunzira Baibulo, tinasintha moyo wathu, tinadzipereka kwa Mulungu ndipo kenako tinabatizidwa. Kuyambira nthawi imeneyo, timafunitsitsa kumvera Mulungu “mochokera pansi pa mtima.” Mwachidule tingati ‘tinamasulidwa ku uchimo n’kukhala akapolo a chilungamo.’ (Aroma 6:17, 18) Komabe tikamachita chilichonse chimene matupi athu ochimwawa akufuna, ndiye kuti ‘tikulola kuti uchimo uzitilamulirabe.’ Anthufe tingathe kulola kapena kukana kuti uchimo uzitilamulira. Ndiye dzifunseni kuti, ‘Kodi ndinafa ku uchimo? Kapena kodi nthawi zina ndimangotsatira mtima wanga komanso thupi lochimwali n’kumachita zinthu zoipa? Kodi ndikukhala ndi moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu?’ Ngati timayamikira kukoma mtima kwa Mulungu, tidzayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa. w16.12 1:11, 12
Lachitatu, August 22
Kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa . . . mtendere.—Aroma 8:6.
Timakhala ndi mtenderewu chifukwa choti timayesetsa kukhala bwino ndi anthu mumpingo komanso m’banja. Timadziwa kuti tonsefe ndi ochimwa choncho mavuto sangalephere. Koma zoterezi zikachitika, timatsatira malangizo a Yesu akuti: “Pita ukayanjane ndi m’bale wako.” (Mat. 5:24) Sizivuta kuthetsa mavuto tikamakumbukira kuti m’bale kapena mlongo wathuyo nayenso akutumikira “Mulungu amene amapatsa mtendere.” (Aroma 15:33; 16:20) Koma palinso mtendere wina wamtengo wapatali umene tili nawo. ‘Tikamaika maganizo pa zinthu za mzimu’ timakhala pa mtendere ndi Mulungu. Pa nkhaniyi, mawu amene Yesaya ananena akukwaniritsidwa masiku ano. Ponena za Yehova, iye analemba kuti: ‘Anthu amene ali ndi mtima wosagwedezeka mudzawateteza powapatsa mtendere wosatha, chifukwa amadalira inu.’—Yes. 26:3; Aroma 5:1. w16.12 2:5, 18, 19
Lachinayi, August 23
Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye.—Afil. 4:4.
Masiku otsiriza ano ndi ovuta koma Yehova akudalitsabe anthu ake. Iye amawasamalira mwauzimu komanso amawathandiza kuti azigwirizana padziko lonse. (Yes. 54:13) Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjeza, Yehova akutidalitsa panopa potipatsa abale, alongo komanso makolo m’gulu lake. (Maliko 10:29, 30) Kuwonjezera pamenepo, anthu amene amafunafuna Mulungu ndi mtima wonse amasangalala, amakhutira ndi zomwe ali nazo komanso amakhala ndi mtendere wa mumtima. (Afil. 4:5-7) Tisamakayikirenso kuti ‘tikamachita chifuniro cha Mulungu, tidzalandira zimene Mulunguyo walonjeza.’ (Aheb. 10:35, 36) Choncho tiyeni tipitirize kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso tizitumikira Yehova ndi mtima wonse. Tikamachita zimenezi sitikayikira ngakhale pang’ono kuti adzatidalitsa.—Akol. 3:23, 24. w16.12 4:17, 20
Lachisanu, August 24
Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.—2 Akor. 3:17.
Kodi munthu amene sakuyenera kuchita zinazake tinganene kuti alidi ndi ufulu? Inde. N’chifukwa chiyani tikutero? Malamulo oletsa anthu kuchita zinthu zinazake amatiteteza. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwasankha kuti mupite kwinakwake kutali pa galimoto. Koma kumene mukupitako kulibe malamulo a pamsewu ndipo aliyense amangoyenda mbali imene akufuna komanso amathamangitsa galimoto mmene akufunira. Kodi mungamve kuti ndinu wotetezeka? Yankho ndi lodziwikiratu. Choncho malamulo amathandiza kuti anthu azisangalala ndi ufulu wawo moyenera. Kuti timvetse bwino mfundoyi, taganizirani chitsanzo cha Adamu. Iye anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wake wosankha zochita. Zimene anachitazi zinabweretsa mavuto aakulu kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Kuganizira mfundoyi kungatithandize kuti tizigwiritsa ntchito moyenera ufulu wathu n’kumapewa kuswa malamulo a Mulungu. w17.01 2:6, 8
Loweruka, August 25
Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.—Aroma 12:3.
Kupemphera komanso kudzifufuza moona mtima kungathandize kuti tisamavomere zinthu zimene sitingakwanitse. Koma nkhani ya Gidiyoni ikhoza kutithandiza tikavomera kuchita utumiki wina umene tapatsidwa. Imatikumbutsa mfundo yoti sitingachite bwino utumiki uliwonse popanda kutsogoleredwa komanso kudalitsidwa ndi Yehova. Paja timalangizidwa kuti: “Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Choncho tikapatsidwa utumiki tizipemphera kwa Yehova. Ndiyeno kuti tidziwe zochita, tizifufuza m’Mawu ake komanso m’malangizo amene gulu lake lapereka. Tikatero timasonyeza kuti tikuzindikira zoti nzeru zathu n’zoperewera poyerekezera ndi za Yehova. Tisamaiwalenso kuti ‘kudzichepetsa kwa Yehova n’kumene kumatikweza’ osati luso lathu. (Sal. 18:35) Tikamayenda modzichepetsa ndi Mulungu tidzapewa kudziona ngati apamwamba kapena ngati osanunkha kanthu. w17.01 3:17, 18
Lamlungu, August 26
Zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.—1 Akor. 15:58.
Yesu ankadziwa kuti adzachoka padzikoli ndipo padzafunika anthu ena oti azigwira ntchito imene ankagwira. Ophunzira ake anali ochimwa koma iye ankawakhulupirira ndipo anawauza kuti adzachita zambiri kuposa zimene iyeyo anachita. (Yoh. 14:12) Iye anawaphunzitsa bwino moti anakwanitsa kulalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Yesu atafa anaukitsidwa n’kupita kumwamba. Kumwambako, anapatsidwa udindo waukulu kwambiri kuposa ‘boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse komanso ambuye onse.’ (Aef. 1:19-21) Tikakhalabe okhulupirika n’kumwalira Aramagedo isanafike, tidzaukitsidwa m’dziko latsopano ndipo tidzakhala ndi ntchito zambiri zosangalatsa. Koma panopa ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira ndi yolalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu. Choncho kaya ndife achikulire kapena achinyamata, tiyeni tiziyesetsa kukhala ndi ‘zochita zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ w17.01 5:17, 18
Lolemba, August 27
Ine ndine Yehova, sindinasinthe.—Mal. 3:6.
Dipo linalipiridwa kale ndipo limafafaniziratu mlandu umene Adamu anatipalamulira. (Aheb. 9:24-26) Timayamikira kwambiri kuti dipo la Khristu limatithandiza kuti tisakhale akapolo a dziko la Satanali ndiponso tisamaope imfa. (Aheb. 2:14, 15) Malonjezo a Mulungu ndi odalirika. Mofanana ndi malamulo ake a m’chilengedwe omwe sasintha, Yehovanso sasintha ndipo sadzatigwiritsa mwala. Kuwonjezera pa mphatso ya moyo, iye amatipatsanso chikondi chake. Paja Baibulo limati: “Ife tikudziwa ndipo tikukhulupirira za chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa ife. Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:16) Dziko lonseli lidzakhala Paradaiso wokongola kwambiri ndipo munthu aliyense azidzatha kukonda kwambiri Mulungu. Tiyeni nafenso tizitsanzira angelo okhulupirika amene amanena kuti: “Mulungu wathu wanzeru, wamphamvu ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemerero ndi ulemu, ndipo ayamikiridwe kwamuyaya. Ame.”—Chiv. 7:12. w17.02 2:16, 17
Lachiwiri, August 28
Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.—2 Akor. 7:1.
Mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1973, munali funso lakuti: “Kodi . . . anthu amene sanasiye kusuta fodya angabatizidwe?” Yankho linali lakuti: “Malemba amasonyeza kuti sayenera kubatizidwa.” Nsanja ya Olonda imeneyi inagwiritsanso ntchito malemba ena posonyeza kuti munthu wosuta fodya amene sakulapa ayenera kuchotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:7) Inatinso: “Awa si maganizo a munthu amene akungofuna kupondereza ena. Koma Mulungu ndi amene akufuna zimenezi ndipo malangizowa ndi ochokera m’Mawu ake.” Posachedwapa buku lina lonena za zipembedzo ku United States linati: “Atsogoleri azipembedzo akhala akusintha mfundo zimene amaphunzitsa n’cholinga choti zizigwirizana ndi maganizo a anthu.” Kodi pali gulu linanso lachipembedzo limene limatsatira Mawu a Mulungu ngakhale pa mfundo zimene likuona kuti anthu ake ena angavutike kuzitsatira? w17.02 4:15
Lachitatu, August 29
Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.—Mat. 23:12.
Akulu amasonyeza kuti ndi abusa odzichepetsa. Umboni wa zimenezi ndi woti amakana kuti anthu aziwachitira zinthu ngati anthu otchuka. Choncho amasiyana ndi atsogoleri ambiri achipembedzo a masiku ano komanso a m’nthawi ya Yesu. Ponena za atsogoleriwo Yesu anati: “Amakonda malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso kupatsidwa moni m’misika.” (Mat. 23:6, 7) Koma abusa achikhristu enieni amakhala odzichepetsa ndipo amamvera mawu a Yesu akuti: “Musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi, wakumwamba Yekhayo. Musamatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu.” (Mat. 23:8-11) Popeza akulu amatsatira malangizowa, n’chifukwa chake abale ndi alongo amawakonda komanso kuwalemekeza kwambiri. w17.03 1:14, 15
Lachinayi, August 30
Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Aliyense ali ndi udindo wosankha zochita ndipo kuti tizisankha zochita mwanzeru tiyenera kudziwa bwino mfundo za m’Malemba. Choncho sitiyenera kupatsa munthu wina udindo wathu wosankha zochita. M’malomwake tiyenera kufufuza kuti tidziwe zimene Mulungu angasangalale nazo, n’kusankha zimenezo. Ngati talola kuyendera maganizo a anthu ena n’kusankha zolakwika, ndiye kuti anthuwo atisankhira zochita. (Miy. 1:10, 15) Koma ndi udindo wathu kusankha zochita mogwirizana ndi chikumbumtima chathu chabwino ngakhale zitakhala kuti ena akutikakamiza kuti tisankhe zinazake. Tikalola kuti ena atisankhire zochita zimakhala ngati tasankha ‘kuyenda nawo limodzi panjira’ yawo. Koma zimenezi zikhoza kutibweretsera mavuto. Mtumwi Paulo anachenjeza Agalatiya za kuipa kolola kuti ena aziwasankhira zochita. (Agal. 4:17) Anthu ena mumpingo ankafuna kuti azisankhira anzawo zochita n’cholinga choti anthuwo azitsatira iwowo osati atumwi. w17.03 2:8-10
Lachisanu, August 31
[Yosiya] akadali mnyamata, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake. M’chaka cha 12 anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu pochotsa malo okwezeka, mizati yopatulika.—2 Mbiri 34:3.
Yosiya ankadzipereka kwambiri pa zinthu zosangalatsa Mulungu. Achinyamata angatsanzire Yosiya n’kuyamba kutumikira Yehova adakali aang’ono. N’kutheka kuti Mfumu Manase italapa inaphunzitsa Yosiya za chifundo cha Yehova. Achinyamatanu, muzigwirizana ndi anthu achikulire a m’banja lanu kapena mumpingo ndipo mungaphunzire zambiri pa zimene Yehova wawachitira. Musaiwalenso kuti Yosiya anakhudzidwa mtima kwambiri atamva mawu a m’Chilamulo ndipo anachitapo kanthu. Inunso mukamawerenga Mawu a Mulungu mungakhale osangalala komanso mungalimbitse ubwenzi wanu ndi iye. Zingakulimbikitseninso kuthandiza ena kuti nawonso ayambe kutumikira Yehova. (2 Mbiri 34:18, 19) Kuphunzira Baibulo panokha kungakuthandizeni kuti muone ngati pali zinthu zina zofunika kusintha kuti muzitumikira bwino Mulungu. Ndipo mukaona kuti zilipodi, muyenera kusintha ngati mmene anachitira Yosiya. w17.03 3:18, 19