September
Loweruka, September 1
Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake.—Yak. 1:4.
M’Baibulo, mawu akuti kupirira amatanthauza zambiri. Mawuwa amatanthauza zimene timaganiza komanso zimene timachita tikakumana ndi mavuto. Munthu wopirira amakhala wolimba mtima, wokhulupirika komanso woleza mtima. Buku lina linati kupirira “n’kukhala ndi mtima wosagonja ukakumana ndi mavuto chifukwa chakuti uli ndi chikhulupiriro cholimba. Khalidweli limathandiza munthu kukhalabe wolimba pamene akukumana ndi mavuto. Munthu wopirira saganizira kwambiri za mavuto amene akukumana nawo koma amaganizira za madalitso amene angapeze akapirira mavutowo.” Akhristufe timapirira chifukwa cha chikondi. (1 Akor. 13:4, 7) Popeza timakonda Yehova, timapirira mavuto onse amene timakumana nawo pochita chifuniro chake. (Luka 22:41, 42) Abale ndi alongo athu akatilakwira chifukwa choti si angwiro, timapirira chifukwa choti timawakonda. (1 Pet. 4:8) Komanso kukonda mwamuna kapena mkazi wathu kumatithandiza kuti tizipirira ‘masautso’ alionse m’banja. Kumatithandizanso kuti tiziyesetsa kulimbitsa banja lathu.—1 Akor. 7:28. w16.04 2:3, 4
Lamlungu, September 2
Iwo anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa. Tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi mogwirizana.—Mac. 2:42.
Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “anapitiriza kulabadira,” amasonyeza kuti ankachita khama kwambiri. Mu ulamuliro wa Aroma sizinali zapafupi kuti Akhristu azisonkhana. Komanso atsogoleri achipembedzo achiyuda ankawatsutsa kwambiri. Komabe iwo sanabwerere m’mbuyo. Masiku ano, pali atumiki a Yehova ambiri amene amaona kuti misonkhano ndi yofunika. Mwachitsanzo, M’bale George Gangas, amene anatumikira m’Bungwe Lolamulira kwa zaka 22, ananena kuti: “Munthune ndimalimbikitsidwa ndikasonkhana ndi abale ndipo ndimasangalala kwabasi. Iye ananenanso kuti: “Maganizo anga onse amakhala pa misonkhano basi.” Kodi inunso mumamva chonchi mukaganizira zosonkhana kuti mulambire Yehova? Ngati ndi choncho, yesetsani kuti musamaphonye misonkhano. Mukatero mudzafanana ndi Mfumu Davide amene analemba kuti: “Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala.”—Sal. 26:8. w16.04 3:16-18
Lolemba, September 3
Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba.—Mat. 5:24.
Tiyerekeze kuti mwazindikira kuti m’bale wina wakhumudwa chifukwa cha zimene munalankhula kapena kuchita. Kodi mungatani? Chofunika n’kukambirana ndi munthuyo. Cholinga si kumuchititsa munthuyo kuona kuti nayenso analakwitsa koma kuvomereza zimene mwalakwitsa n’kukhazikitsa mtendere. Paja chofunika kwambiri n’kukhala pa mtendere ndi Akhristu anzathu. Abulahamu ndi Loti anali ndi ziweto ndipo abusa awo ankakanganira malo odyetsera ziwetozo. Abulahamu anauza Loti kuti ayambe kusankha malo amene angakonde kukhala ndi banja lake. (Gen. 13:1, 2, 5-9) Apatu Abulahamu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Iye sanaganizire zofuna zake koma ankangofuna kukhazikitsa mtendere. Kodi iye anavutika chifukwa chopereka mwayi kwa Loti? Ayi. Izi zitangochitika, Yehova anamulonjeza kuti adzamudalitsa. (Gen. 13:14-17) Yehova sangalole kuti mtumiki wake avutike kwambiri chifukwa choti watsatira mfundo za m’Malemba pothetsa kusamvana. w16.05 1:11, 12
Lachiwiri, September 4
Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.—Aef. 5:17.
M’Baibulo muli malamulo osiyanasiyana amene Yehova watipatsa. Mwachitsanzo, Yehova amaletsa chiwerewere, kulambira mafano, kuba komanso kuledzera. (1 Akor. 6:9, 10) Komanso Mwana wake, Yesu Khristu anatipatsa lamulo lakuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Tikamatsatira malamulowa zinthu zimatiyendera bwino. Mwachitsanzo, timakhala ndi moyo wabwino, timakhala ndi banja losangalala komanso anthu amatilemekeza. Koma chofunika kwambiri n’choti Yehova amasangalala nafe ndiponso amatidalitsa. w16.05 3:1
Lachitatu, September 5
Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma 12:2.
Tikamatsogoleredwa ndi mzimu woyera komanso kuyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera, zoganiza zathu, mawu athu komanso zochita zathu zimakhala zabwino. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Koma ngakhale titafika pamenepa, tiyenera kusamalabe kuti tisayambirenso kuchita makhalidwe olakwika amene tinasiya. (Miy. 4:23) Ngati tikuona kuti zikutivuta kusintha, tisataye mtima chifukwa zimatenga nthawi ndithu. Paja nkhani yovala umunthu watsopano siitha. Tiyenera kukhala oleza mtima n’kumalola kuti Baibulo lizitithandiza kusintha. Mwina poyamba zingamativute kwambiri kuti tizichita zimene Baibulo limanena. Koma pang’ono ndi pang’ono tingayambe kuganiza komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu amafuna.—Sal. 37:31; Miy. 23:12; Agal. 5:16, 17. w16.05 4:14, 16
Lachinayi, September 6
Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.—Sal. 1:2.
Masiku ano Yehova amaumba atumiki ake pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu woyera komanso mpingo wachikhristu. Mawu a Mulungu amatiumba ngati timawawerenga, kusinkhasinkha mfundo zake komanso kupempha Yehova kuti atithandize kuzigwiritsa ntchito. Davide analemba kuti: “Ndikakumbukira inu ndili pabedi langa, pa nthawi za ulonda wa usiku ndimasinkhasinkha za inu.” (Sal. 63:6) Analembanso kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.” (Sal. 16:7) Davide ankalola kuti malangizo a Mulungu akhazikike mumtima mwake komanso kuti aumbe maganizo ake. Iye ankachita zimenezi ngakhale kuti malangizo ena anali omudzudzula. (2 Sam. 12:1-13) Davide anapereka chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa komanso kumvera Mulungu. Kodi inunso mumasinkhasinkha Mawu a Mulungu, n’kulola kuti zimene mwawerengazo zikhazikike mumtima mwanu? Tiyenera kumachita zimenezi nthawi zonse.—Sal. 1:3. w16.06 1:11
Lachisanu, September 7
Usamafulumire kukwiya mumtima mwako.—Mlal. 7:9.
Tizikumbukira kuti anthu anasiya kukhala angwiro zaka 6,000 zapitazo, choncho tonse timalakwitsa zinthu zambiri. Ndiye si bwino kuyembekezera kuti ena azichita bwino chilichonse. Si nzerunso kusiya kusangalala ndi Akhristu anzathu chifukwa cha zolakwa za ena. Kungakhalenso kulakwa kwambiri ngati titafika posiya gulu la Yehova chifukwa chokhumudwa. Tikutero chifukwa chakuti zimenezi zingatitayitse mwayi wotumikira Mulungu komanso wodzapeza moyo wosatha m’dziko latsopano. Kuti tizikhalabe osangalala komanso tisataye mtima, tiyenera kukumbukira lonjezo la Yehova lakuti: “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” (Yes. 65:17; 2 Pet. 3:13) Tiyeni tisalole kuti zolakwa za ena zitilepheretse kudzalandira madalitso amenewa. w16.06 4:13, 14
Loweruka, September 8
Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.—Deut. 6:4.
Mawu oti “Yehova mmodzi” amatanthauzanso kuti zolinga ndi zochita zake sizisintha. Iye sasinthasintha kapena kulonjeza zina n’kuchita zina. Nthawi zonse ndi wokhulupirika ndipo amanena zoona. Mwachitsanzo, iye anauza Abulahamu kuti ana ake adzakhala m’Dziko Lolonjezedwa ndipo anachita zozizwitsa kuti akwaniritse lonjezoli. Ngakhale kuti panadutsa zaka 430, iye anakwaniritsabe zimene analonjezazo. (Gen. 12:1, 2, 7; Eks. 12:40, 41) Patapita zaka mahandiredi angapo, Yehova anauza Aisiraeli kuti iwo ndi mboni zake ndipo ananena kuti: “Ine sindinasinthe. Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa.” Ananenanso kuti: “Nthawi zonse ine sindisintha.” (Yes. 43:10, 13; 44:6; 48:12) Kunena zoona, Aisiraeli komanso ifeyo tili ndi mwayi wolambira Mulungu amene sasintha ndipo ndi wodalirika nthawi zonse.—Mal. 3:6; Yak. 1:17. w16.06 3:6, 7
Lamlungu, September 9
Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.—Maliko 13:33.
Masiku ano, mayiko ambiri ali ndi asilikali olondera m’malire komanso zipangizo zamakono zachitetezo. Amachita izi kuti aziona zigawenga kapena adani ofuna kulowa m’dziko lawo. Koma mabomawa sadziwa zoti pali boma lamphamvu kumwamba lolamulidwa ndi Yesu. Bomali lidzawononga maboma onse padzikoli. (Yes. 9:6, 7; 56:10; Dan. 2:44) Koma ifeyo timayesetsa kukhala maso kuti tsiku la Yehova lidzatipeze tili okonzeka. (Sal. 130:6) Pamene mapeto akuyandikira zizikhala zovuta kwambiri kuti tikhalebe maso. Koma zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati tingayambe kugona. w16.07 2:2, 9, 10
Lolemba, September 10
Kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anandisonyeza sikunapite pachabe.—1 Akor. 15:10.
Paulo ankadziwa kuti kunali kosayenera kuti Mulungu amusonyeze chifundo chachikulu chifukwa chakuti poyamba ankazunza Akhristu. Chakumapeto kwa moyo wake analembera Timoteyo kuti: “Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupirika, ndipo anandipatsa utumiki.” (1 Tim. 1:12-14) Kodi Paulo ankanena za utumiki uti? Iye anauza akulu a ku Efeso kuti: “Moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi. Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (Mac. 20:24) Paulo ankachita utumiki wake modzipereka ndipo ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe. Komanso iye anasonyeza kuti kukoma mtima kumene Mulungu anamusonyeza “sikunapite pachabe.” w16.07 4:1-3
Lachiwiri, September 11
Ndidzayembekezera moleza mtima.— Mika 7:7.
Nthawi zina tingafunike kuyembekezera kaye kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino kapena kuti tikhale pa udindo winawake. Komabe tiyenera kukumbukira kuti nthawi zonse Yehova amathandiza atumiki ake. Iye analonjeza Abulahamu kuti adzakhala ndi mwana, komabe Abulahamu anayenera kuyembekezera. (Aheb. 6:12-15) Ngakhale kuti panadutsa zaka zambiri, Abulahamu sanataye mtima ndipo Yehova anakwaniritsadi lonjezo lake pamene Abulahamuyo anabereka Isaki. (Gen. 15:3, 4; 21:5) Kuyembekezera n’kovuta. (Miy. 13:12) Ndipo munthu akamangoganizira zokhumudwitsa, akhoza kutaya mtima. Choncho pa nthawi imene mukuyembekezerayo, muziyesetsa kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kusinkhasinkha, timakhala anzeru, oganiza bwino komanso ozindikira. Timadziwanso zambiri ndipo timasankha zochita mwanzeru. Tsiku lililonse timafunika kusankha zochita pa nkhani zokhudza zosangalatsa, zovala, kudzikongoletsa, kugwiritsa ntchito ndalama komanso kukhala bwino ndi anthu. Tikamagwiritsa ntchito zimene timaphunzira m’Baibulo, tingathe kusankha zinthu zimene Yehova amasangalala nazo. w16.08 3:9-11
Lachitatu, September 12
Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu.—Afil. 2:13.
Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamaleki ndi Aitiyopiya komanso anapatsa mphamvu Nehemiya ndi anzake kuti amalize ntchito yawo. Iye angatithandizenso ifeyo kuti tizilalikirabe m’gawo lovuta ndiponso tisamafooke tikamatsutsidwa kapena tikakhala ndi nkhawa. (1 Pet. 5:10) Sitiyembekezera kuti Yehova azitichitira zozizwitsa. M’malomwake tiyenera kuchita khama pa zinthu monga kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kukonzekera ndi kupezeka pamisonkhano. Tiziphunziranso Baibulo patokha, kuchita kulambira kwa pabanja ndiponso kupemphera. Tisamalole chilichonse kutilepheretsa kuchita zinthu zimene Yehova amagwiritsa ntchito potilimbikitsa komanso kutipatsa mphamvu. Ngati mukuona kuti simukuchita bwino pambali zina zimene tatchulazi, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Mukatero, mzimu wa Mulungu ‘udzalimbitsa zolakalaka zanu’ kuti muchite zinthu zimene iye amakonda. w16.09 1:12
Lachinayi, September 13
Chifukwa cha kuwanda kwa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.—1 Akor. 7:2.
Mtumwi Paulo ananena kuti kusakhala pa banja n’kwabwino koma iye ananenanso mawu amulemba la leroli. Ndiye anapitiriza kuti: “Ngati sangathe kudziletsa, akwatire, pakuti ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kuvutika ndi chilakolako.” Komabe munthu asanaganize zolowa m’banja, ayenera kuganiziranso za zaka zake popeza Paulo anati: “Ngati wina akuona kuti zikumuvuta kukhalabe yekha, ngati wapitirira pachimake pa unyamata, ndipo ngati ziyenera kutero, achite mmene akufunira, sachimwa. Akwatire.” (1 Akor. 7:9, 36; 1 Tim. 4:1-3) N’zoona kuti kukhala pa banja kungathandize munthu kupewa chiwerewere kapena chizolowezi choseweretsa maliseche. Komabe munthu sayenera kukwatira kapena kukwatiwa chifukwa cha chilakolako chimene chimakhala champhamvu pa zaka zaunyamata. Pa nthawiyi angakhale adakali wamng’ono moti sangathe kusamalira banja. w16.08 1:17
Lachisanu, September 14
Tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.—2 Akor. 6:4.
Anthu amatha kutiganizira zinthu zosiyanasiyana chifukwa cha mmene tikuonekera. (1 Sam. 16:7) Popeza timatumikira Mulungu, sitimangovala chilichonse chimene chatisangalatsa. Mfundo zimene timaphunzira m’Baibulo zimatithandiza kuti tizipewa kuvala zothina, zoonekera mkati kapena zochititsa anthu kuganiza zachiwerewere. Komanso si bwino kuvala zovala zimene zingaonetse kapena kudinda malo obisika. Zovala zathu zisamachititse anthu ena kuyang’ana kumbali. Tikadzikongoletsa moyenera komanso kuvala zovala zaukhondo ndi zaulemu, anthu ambiri amatilemekeza. Izi zingachititse kuti nawonso ayambe kulambira Mulungu. Komanso tikamavala bwino anthu amalankhula zabwino zokhudza gulu lathu. Zimenezi zingapangitsenso kuti anthu azimvetsera uthenga wathu. w16.09 3:5, 6
Loweruka, September 15
Akhale ololera, ndi ofatsa kwa anthu onse.—Tito 3:2.
Musamafulumire kuganiza kuti mukudziwa zimene anthu ena amakhulupirira. Anthu ena amakhulupirira zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina, koma amakhulupiriranso kuti Mulungu alipo. Amakhulupirira kuti Mulungu anangochititsa kuti zinthu zina zisinthe n’kukhala zamoyo zosiyanasiyana. Ndiye pali ena amene amakhulupirira kuti mfundo yakuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina ikanakhala yabodza, si bwenzi ikuphunzitsidwa kusukulu. Pomwe ena anasiya kukhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa choti anakhumudwa ndi zipembedzo. Choncho musanayambe kukambirana ndi munthu zokhudza mmene moyo unayambira, ndi bwino kumufunsa kaye mafunso kuti mudziwe zimene amakhulupirira. Mukamamvetsera pamene iye akufotokoza, zingapangitse kuti nayenso amvetsere inuyo mukamafotokoza. Kodi mungatani ngati munthu wanena kuti ndinu wopusa chifukwa mumakhulupirira kuti kuli Mlengi? Mwina mungamufunse kuti: ‘Kodi inuyo mumakhulupirira kuti moyo unayamba bwanji?’ Ndiyeno munganene kuti, ‘Mogwirizana ndi sayansi, ngati zamoyo zinayambira ku zinthu zina, ndiye kuti chinthu choyambacho chinafunika kubereka ana.’ Katswiri wina anati: “Munthu amagoma akaona mmene moyo unayambira, ngakhale wa tinthu ting’onoting’ono.” w16.09 4:12, 13
Lamlungu, September 16
Sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambiri.—Aheb. 11:35.
Sitikudziwa kuti apa Paulo ankanena za ndani. Koma pali anthu monga Naboti komanso Zekariya amene anaponyedwa miyala mpaka kufa chifukwa choti anamvera Mulungu komanso ankachita chifuniro chake. (1 Maf. 21:3, 15; 2 Mbiri 24:20, 21) Nayenso Danieli ndi anzake akanatha ‘kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe.’ Koma chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro cholimba, sanachite zimenezi ndipo tingati “anatseka mikango pakamwa” komanso “anagonjetsa mphamvu ya moto.” (Aheb. 11:33, 34; Dan. 3:16-18, 20, 28; 6:13, 16, 21-23) Chifukwa cha chikhulupiriro, aneneri monga Mikaya ndi Yeremiya ‘analandira mayesero awo mwa kutonzedwa komanso kuikidwa m’ndende.’ Ena monga Eliya “anayenda uku ndi uku m’zipululu, m’mapiri, m’mapanga, ndi m’maenje a dziko lapansi.” Onsewa anakhalabe okhulupirika chifukwa anali ndi “chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.”—Aheb. 11:1, 36-38; 1 Maf. 18:13; 22:24-27; Yer. 20:1, 2; 28:10, 11; 32:2. w16.10 3:10, 11
Lolemba, September 17
Modzichepetsa, muziona ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.
Ifenso tingasonyeze kukoma mtima tikamayesetsa kupereka moni kwa alendo ku Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina alendo amachita manyazi ndipo amangokhala paokha. Zinthu zimene anthu ena amakumana nazo zimawachititsa kuganiza kuti mtundu wawo ndi wosanunkha kanthu poyerekezera ndi mitundu ina. Choncho tiyenera kuyesetsa kuwalandira mwansangala komanso mokoma mtima. Ngati n’zotheka, mungapite pa JW Language kuti muphunzire moni wa zinenero zosiyanasiyana. (Afil. 2:4) Mwina inuyo mumachita manyazi kulankhula ndi anthu a mitundu ina. Ngati ndi choncho, poyambira pabwino n’kungowafotokozera zinthu zina zokhudza inuyo. Mudzadabwa kuona kuti mukufanana nawo pa zinthu zambiri ndipo mudzazindikira kuti chikhalidwe chilichonse chili ndi ubwino komanso kuipa kwake. w16.10 1:13, 14
Lachiwiri, September 18
Mbiri yamvekatu kuti pakuchitika dama pakati panu, ndipo dama lake ndi loti ngakhale anthu a mitundu ina sachita.—1 Akor. 5:1.
Tikamatsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu tingathandize kuti mpingo ukhale woyera. Taganizirani zimene zinachitika mumpingo wa Korinto wakale. Paulo anadzipereka kwambiri kulalikira mumzinda wa Korinto komanso ankakonda Akhristu akumeneko. (1 Akor. 1:1, 2) Ndiye mukuganiza kuti anamva bwanji atazindikira kuti m’bale wina ankachita chiwerewere ndipo akulu ankangomulekerera? Paulo analangiza akuluwo kuti apereke munthuyu kwa Satana kapena kuti amuchotse mumpingo. Kuti mpingo ukhalebe woyera akuluwo anayenera kuchotsa “chofufumitsa.” (1 Akor. 5:5-7, 12) Tikamatsatira malangizo a Yehova pa nkhani ya ochotsedwa, timathandiza kuti mpingo ukhale woyera. Izi zimathandizanso kuti munthuyo alape n’kupempha Yehova kuti amukhululukire. w16.11 2:14
Lachitatu, September 19
Ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.—Mac. 13:15.
Zimene ananena mnyamata wina dzina lake Rubén zikusonyeza kuti kulimbikitsa ena n’kofunika kwambiri. Iye anati: “Kwa zaka zambiri ndakhala ndikudziona kuti ndine wosafunika. Koma tsiku lina ndili mu utumiki, mkulu amene ndinayenda naye anazindikira kuti sindikusangalala. Nditayamba kumufotokozera mavuto anga komanso mmene ndinkamvera, anamvetsera mwachidwi. Kenako anandikumbutsa za zinthu zabwino zimene ndakwanitsa kuchita. Anandikumbutsanso mawu a Yesu oti munthu ndi wofunika kuposa mpheta zambiri. Ndimakumbukirabe lemba limeneli ndipo limandikhudza mtima kwambiri. Zimene mkuluyu ananena zinandilimbikitsa kwambiri.” (Mat. 10:31) M’pake kuti Baibulo limatsindika kufunika koti tizilimbikitsana nthawi zonse. Mtumwi Paulo analembera Akhristu achiheberi kuti: “Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro. M’malomwake, pitirizani kudandaulirana [kapena kuti kulimbikitsana] tsiku ndi tsiku, . . . kuopera kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chingaumitse mtima wa wina wa inu.” (Aheb. 3:13) Tingathe kumvetsa kuti malangizo oti tizilimbikitsanawa ndi ofunikadi, tikaganizira mmene tinamvera munthu wina atatilimbikitsa. w16.11 1:2, 3
Lachinayi, September 20
Pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.—Mac. 20:30.
M’chaka cha 313 C.E., mfumu ina ya Aroma dzina lake Constantine inapangitsa kuti chipembedzo chophunzitsa zabodzachi chikhale chovomerezeka ndi boma. Mwachitsanzo, nthawi ina Constantine anachititsa msonkhano wa atsogoleri achipembedzo. Msonkhanowo utatha, iye anathamangitsa m’dzikolo wansembe wina dzina lake Arius chifukwa choti anakana kuvomereza kuti Yesu ndi Mulungu. Patapita nthawi, Theodosius anakhala mfumu ya Aroma ndipo tchalitchi cha Katolika chinakhala chipembedzo chachikulu mu ufumu wa Roma. Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti Aroma anayamba kudzitchula kuti ndi Akhristu mu ulamuliro wa Mfumu Theodosius. Koma zoona n’zakuti pa nthawiyi, Akhristu ampatuko anali atayamba kutsatira ziphunzitso zachikunja choncho anali mbali ya Babulo Wamkulu. Komabe panali Akhristu odzozedwa okhulupirika omwe anali ngati tirigu amene Yesu anatchula. Akhristu okhulupirikawa ankayesetsa kulambira Mulungu koma anthu sankamvetsera zimene ankaphunzitsa.—Mat. 13:24, 25, 37-39. w16.11 4:8, 9
Lachisanu, September 21
Mutulireni [Yehova] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.—1 Pet. 5:7.
Tikukhala m’nthawi yovuta ndipo zinthu zodetsa nkhawa ndi zambiri. Satana ndi wokwiya kwambiri ndipo “akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:17) Choncho n’zosadabwitsa kuti ngakhale atumiki a Yehovafe nthawi zina timakhala ndi nkhawa. Ndipotu atumiki akale monga Mfumu Davide ‘ankalimbana ndi masautso.’ (Sal. 13:2) Tisaiwalenso kuti mtumwi Paulo ‘ankadera nkhawa mipingo yonse.’ (2 Akor. 11:28) Ndiye kodi tingatani ngati tikuda nkhawa ndi zinazake? Tizipemphera kuchokera mumtima, tiziwerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuwasinkhasinkha, tizipempha mzimu wa Mulungu komanso tizifotokozera munthu amene angatithandize. Atate wathu wakumwamba anathandiza atumiki ake m’mbuyomo kuti achepetse nkhawa ndipo angatithandizenso ifeyo. w16.12 3:1, 2
Loweruka, September 22
Pothera pake pa zinthu zimenezo ndi imfa.—Aroma 6:21.
M’nthawi ya atumwi, anthu ena a ku Korinto anali akuba, achigololo, oledzera, olambira mafano ndiponso ankagonana ndi amuna kapena akazi anzawo. Koma atadziwa Mulungu n’kuyamba kumukonda, anasinthiratu ndipo ankachita manyazi akaganizira zimene ankachita poyambazo. (Aroma 6:21; 1 Akor. 6:9-11) Nawonso Akhristu a ku Roma ankafunika kusintha. Paulo anawauza kuti: “Musapereke ziwalo zanu ku uchimo kuti zikhale zida zochitira zinthu zosalungama, koma dziperekeni kwa Mulungu monga anthu amene auka kwa akufa. Ziwalo zanunso muzipereke kwa Mulungu monga zida zochitira chilungamo.” (Aroma 6:13) Paulo ankadziwa kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kukhoza kuthandiza Aromawo kukhala oyera. w16.12 1:13
Lamlungu, September 23
Khulupirira Yehova.—Sal. 37:3.
Yehova anatipatsa luso lapadera kwambiri. Luso lake ndi lotha kuganiza. Izi zimatithandiza kuti tizithana ndi mavuto komanso kukonzekera zam’tsogolo. (Miy. 2:11) Iye anatipatsanso luso loti tizitha kukhala ndi mapulani komanso zolinga n’kumazikwaniritsa. (Afil. 2:13) Yehova anatipatsanso chikumbumtima chimene chimatithandiza kudziwa zinthu zoyenera ndi zosayenera. Izi zimatithandiza kuti tizipewa kuchita zoipa komanso kuti tizikonza zimene talakwitsa. (Aroma 2:15) M’Mawu ake timapezamo malangizo komanso mfundo zambiri zotilimbikitsa kuti tizigwiritsa ntchito bwino luso limene iye watipatsa. Mwachitsanzo, m’Malemba Achiheberi timapezamo mfundo yakuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” Komanso muli malangizo akuti: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.” (Miy. 21:5; Mlal. 9:10) M’Malemba Achigiriki timapezanso mawu oti: “Ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino.” Komanso akuti: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana.” (Agal. 6:10; 1 Pet. 4:10) Izi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizichita zinthu zimene zingathandize ifeyo komanso anthu ena. w17.01 1:1, 2
Lolemba, September 24
Zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.—1 Akor. 10:11.
Anthu onse anatengera uchimo ndi imfa kwa Adamu ndi Hava. Ngakhale zili choncho, iwo ali ndi ufulu wosankha zochita. Umboni wa zimenezi ndi mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi mtundu wa Isiraeli. Kudzera mwa Mose, Yehova anapatsa Aisiraeli mwayi wosankha kukhala anthu ake apadera kapena ayi. (Eks. 19:3-6) Ndiye kodi iwo anatani? Anasankha kukhala anthu a Mulungu ndipo anavomera kuti azimvera malamulo ake. Iwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.” (Eks. 19:8) Koma n’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi Aisiraeli anayamba kugwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha zochita ndipo sanatsatire mawu awowa. Tingaphunzire zambiri kwa Aisiraeliwa. Tiyeni tiziyamikira mphatso ya ufulu wosankha imene Yehova anatipatsa. Tiziyesetsa kukhalabe naye pa ubwenzi komanso kumumvera. w17.01 2:9
Lachiwiri, September 25
Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.—Mika 6:8.
Pa nthawi imene Yerobowamu ankalamulira ku Isiraeli, Yehova anatumiza mneneri wa ku Yuda kuti akamuuze uthenga wa chiweruzo. Anachita izi chifukwa chakuti Yerobowamuyo ankachita zoipa. Mneneriyo anachita zinthu modzichepetsa n’kupereka uthengawo. Yerobowamu anakwiya kwambiri koma Yehova anateteza mneneri wakeyo. (1 Maf. 13:1-10) Mneneriyu akubwerera kwawo, anakumana ndi munthu wokalamba wochokera ku Beteli. Munthuyo ananena kuti nayenso ndi mneneri wa Yehova. Ndiyeno anapusitsa mneneriyo kuti asamvere malangizo a Yehova akuti: “Usakadye chakudya kapena kumwa madzi, ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.” Yehova sanasangalale ndipo mneneriyu asanafike kwawo anaphedwa ndi mkango. (1 Maf. 13:11-24) Koma n’chifukwa chiyani mneneriyu anadzikuza n’kutsatira zimene munthu wokalambayo ananena? Baibulo silinena chifukwa chake. Koma n’kutheka kuti anaiwala mfundo yoti ankayenera ‘kuyenda modzichepetsa ndi Yehova.’ w17.01 4:1-3
Lachitatu, September 26
Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita. Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.—Yes. 46:11.
Baibulo limayamba ndi mawu akuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Gen. 1:1) Pa zinthu zimene Yehova analenga timangodziwapo zochepa chabe. (Mlal. 3:11) Mwachitsanzo, sitidziwa bwinobwino zokhudza kuwala, zinthu zimene zili m’mlengalenga komanso mphamvu imene imathandiza dziko kuti likhazikike m’malere. Koma Yehova watithandiza kuti tidziwe chifukwa chimene analengera dziko komanso anthu. Iye analenga dziko kenako analenga anthu m’chifanizo chake kuti azikhala m’dzikoli. (Gen. 1:26) Iye ankafuna kuti akhale Bambo ndipo anthu akhale ana ake. Koma chaputala 3 cha buku la Genesis chimasonyeza kuti Satana anafuna kusokoneza cholinga cha Mulungu. (Gen. 3:1-7) Komabe zimenezi sizinatheke chifukwa palibe amene angalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake. (Yes. 46:10; 55:11) Choncho cholinga choyambirira cha Mulungu chidzakwaniritsidwa pa nthawi yake ndendende. w17.02 1:1, 2
Lachinayi, September 27
Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa [Mose]?—Yes. 63:11.
Popeza mzimu woyera suoneka, kodi Aisiraeli akanadziwa bwanji kuti Mose ankatsogoleredwa ndi mzimu? Mzimu woyera unamuthandiza kuti achite zodabwitsa komanso kuti auze Farao za dzina la Yehova. (Eks. 7:1-3) Unamuthandizanso kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, kufatsa komanso kuleza mtima. Makhalidwewa ndi amene anamuthandiza kuti azitsogolera bwino Aisiraeli. Panali umboni wokwanira woti Yehova anasankha Mose kuti azitsogolera anthu ake. Patapita nthawi, mzimu woyera unathandizanso anthu ena amene Mulungu anawasankha kuti azitsogolera anthu ake. Mwachitsanzo, “Yoswa mwana wa Nuni anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru.” (Deut. 34:9) “Gidiyoni anagwidwa ndi mzimu wa Yehova.” (Ower. 6:34) Ndiponso “mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide.” (1 Sam. 16:13) Anthu onsewa ankadalira mzimu woyera ndipo unkawathandiza kuchita zinthu zimene sakanakwanitsa paokha.—Yos. 11:16, 17; Ower. 7:7, 22; 1 Sam. 17:37, 50. w17.02 3:3-5
Lachisanu, September 28
Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.—2 Akor. 1:24.
Paulo anali chitsanzo chabwino pa nkhani yolemekeza ufulu wa abale ake wosankha okha zochita. Masiku anonso akulu akamapereka malangizo pa nkhani imene munthu ayenera kusankha yekha, ayenera kutengera chitsanzo cha Paulo. Iwo angakambirane ndi munthuyo mfundo za m’Malemba. Komabe amalola kuti munthuyo asankhe yekha zochita. Zimenezi n’zomveka chifukwa munthuyo ndi amene adzakumane ndi zotsatira za zimene angasankhezo. Choncho mfundo yoti tonse tiziikumbukira ndi yakuti: Tikhoza kuthandiza anthu kumvetsa malangizo a M’Baibulo amene angawathandize, koma tisamaiwale kuti udindo wosankha ndi wawo. Akasankha zochita mwanzeru, zinthu zingawayendere bwino. Ndipotu tiyenera kupewa chizolowezi choganiza kuti tili ndi mphamvu zosankhira abale ndi alongo athu zochita. w17.03 2:11
Loweruka, September 29
Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera.—Aheb. 13:17.
Kapolo wokhulupirika wasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro champhamvu polimbikitsa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Kodi inuyo muli m’gulu la nkhosa zina zimene zikuthandiza odzozedwa pa ntchito yofunikayi? Dziwani kuti mudzasangalala kwambiri Mtsogoleri wathu Yesu akadzakuuzani kuti: “Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munachitira ine amene.” (Mat. 25:34-40) Yesu atabwerera kumwamba sanaiwale otsatira ake. (Mat. 28:20) Iye akudziwa mmene mzimu woyera, angelo komanso Mawu a Mulungu anamuthandizira padzikoli kuti atsogolere bwino anthu. Choncho akuthandiza kapolo wokhulupirika pogwiritsa ntchito zinthu zomwezi. Odzozedwa amene ali m’gulu la kapoloyu “amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.” (Chiv. 14:4) Ndiyeno tikamatsatira malangizo a kapolo timakhala tikutsatira Mtsogoleri wathu Yesu. Posachedwapa, Yesu adzatitsogolera polowa m’dziko latsopano n’kulandira moyo wosatha. (Chiv. 7:14-17) Palibe mtsogoleri aliyense padzikoli amene angatilonjeze moyo umenewu. w17.02 4:17-19
Lamlungu, September 30
Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.—Sal. 37:5.
Nthawi zambiri tikakumana ndi mavuto amene tikuona kuti sitingathane nawo patokha, zimakhala zosavuta kudalira Yehova. Koma kodi timadaliranso Yehova pa zinthu zing’onozing’ono zimene timakumana nazo tsiku ndi tsiku kapena timangodalira nzeru zathu? Nanga kodi timafufuza mfundo za m’Baibulo posonyeza kuti tikudalira Yehova? Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti mukutsutsidwa ndi achibale anu kuti musamapite kumisonkhano yampingo kapena ikuluikulu. Mwina mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita. Ndiyeno tiyerekezenso kuti mwachotsedwa ntchito ndipo mukuvutika kupeza ina. Kenako mukulankhula ndi bwana wina amene akufuna kuti akulembeni ntchito. Kodi mungamufotokozere zoti adzafunika kumakupatsani nthawi yosonkhana m’kati mwa mlungu? Kapena simunganene poopa kuti sakulembani? Pa vuto lililonse limene tingakumane nalo, tingachite bwino kutsatira malangizo a wamasalimo amulemba la lero. w17.03 4:6