October
Lolemba, October 1
Anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo. Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.—Sal. 145:19.
Yehova ‘amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amatitonthoza.’ (Aroma 15:5) Iye amadziwa chibadwa chathu komanso zimene tikukumana nazo ndipo amamvetsa mmene tikumvera mumtima mwathu. Amadziwanso bwino zinthu zimene zingatithandize. Koma kodi Mulungu amayankha bwanji tikamupempha kuti atipatse mphamvu kuti tithe kupirira? Tikapempha Yehova kuti atithandize kupirira mayesero, iye ‘amapereka njira yopulumukira.’ (1 Akor. 10:13) Kodi ndiye kuti Yehova amachotsa mayesero athuwo? Nthawi zina amachotsadi. Koma nthawi zambiri amangotithandiza kuti ‘tithe kupirira.’ Yehova amatipatsa mphamvu kuti ‘tithe kupirira zinthu zonse, tikhale oleza mtima ndiponso tikhale achimwemwe.’ (Akol. 1:11) Popeza amadziwa zinthu zimene sitingakwanitse, sangalole kuti vuto likule mpaka kufika poti sitingathe kukhalabe okhulupirika. w16.04 2:5, 6
Lachiwiri, October 2
Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.—Mat. 22:21.
Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizimvera olamulira. Koma amanenanso kuti tiyenera kumvera Mulungu osati anthu. (Mac. 5:29; Tito 3:1) Kodi mfundo zimenezi zikutsutsana? Ayi. Yesu anatchula mfundo yamulemba la leroli imene ingatithandize kudziwa zoyenera kuchita pa nkhaniyi. Kodi tingatsatire bwanji malangizo amenewa? Tiyenera kumvera olamulira polemekeza akuluakulu a boma, kukhoma misonkho komanso kutsatira malamulo amene anakhazikitsa. (Aroma 13:7) Koma olamulira akatiuza kuti tiphwanye malamulo a Mulungu, tiyenera kukana mwaulemu. Tiyeneranso kupewa kulowerera ndale. (Yes. 2:4) Choncho sititsutsa boma kapena kulimbikitsa anthu kuti azikonda kwambiri dziko lawo. (Aroma 13:1, 2) Sitivota, sitiima pa chisankho ndipo sitiyesa kusintha zinthu m’boma. w16.04 4:1, 2
Lachitatu, October 3
Akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina.—Mat. 18:17.
Nthawi zambiri nkhani zimene Akhristu amasemphana maganizo zimakhala zoti angazithetse paokha. Koma Yesu ananenanso kuti nkhani zina n’zofunika kuuza mpingo. (Mat. 18:15-17) Komano kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu wolakwayo sakuvomereza kuti walakwa pamaso pa m’bale wakeyo, mboni za nkhaniyo komanso mpingo? Malinga ndi lembali, munthuyo ayenera kuonedwa ngati “wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.” Masiku ano tinganene kuti munthuyo ayenera kuchotsedwa mumpingo. Nkhani zimene Yesu ananena pa Mateyu 18:15-17, ziyenera kukhala zikuluzikulu osati kungosemphana maganizo ndi munthu wina. Mwina zingakhale zokhudza chinyengo kapena miseche imene inaipitsa mbiri ya munthu wina. w16.05 1:14
Lachinayi, October 4
Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.—Aef. 5:17.
Pali nkhani zambiri zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake. Mwachitsanzo, palibe malamulo onena za zovala zoyenera kwa Akhristu. Zimenezi zimasonyeza kuti Yehova ndi wanzeru. Tikutero chifukwa zikhalidwe zimasiyana, komanso masitayilo a zovala amasintha mogwirizana ndi nthawi. Choncho m’Baibulo mukanakhala mndandanda wa masitayilo oyenera kwa Akhristu, anthu akanasiya kukonda masitayilo amenewo pasanapite nthawi yaitali. N’chifukwa chakenso m’Baibulo mulibe malamulo onena za ntchito zimene tingagwire, thandizo lamankhwala lomwe tingalandire komanso zosangalatsa zimene tiyenera kuchita. Ndiye kodi tingasankhe bwanji zochita pa nkhani zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake? Zikatere, sitiyenera kungosankha zimene tikufuna. M’malomwake tiyenera kufufuza mfundo zonse zokhudza nkhaniyo kenako n’kusankha zimene Yehova angasangalale nazo.—Sal. 37:5. w16.05 3:2, 6
Lachisanu, October 5
Simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.—1 Ates. 2:13.
Mkhristu aliyense ayenera kuti ali ndi mabuku a m’Baibulo amene amawakonda kwambiri. Ena amakonda Mauthenga Abwino chifukwa akawerenga zimene Yesu anachita amaphunzira makhalidwe a Yehova. (Yoh. 14:9) Pomwe ena amakonda mabuku a maulosi ngati Chivumbulutso chifukwa amafotokoza “zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.” (Chiv. 1:1) Ndiye palinso ena amene amakonda kwambiri Masalimo ndi Miyambo chifukwa muli malangizo othandiza. Zonsezi zikusonyeza kuti Baibulo ndi buku la anthu onse. Timakondanso zinthu zothandiza kuphunzira Baibulo zimene gulu limatulutsa. Mwachitsanzo timayamikira kwambiri mabuku, timabuku, magazini komanso zinthu zina zimene timalandira. Zinthuzi zimathandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, tikhale maso komanso kuti tikhale ndi ‘chikhulupiriro cholimba.’—Tito 2:2. w16.05 5:1-3
Loweruka, October 6
Koma makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa. Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.—Agal. 5:22, 23.
Mzimu woyera umatiumba m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ungatithandize kutsanzira Khristu n’kukhala ndi makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. Khalidwe lina limene mzimu woyera umatulutsa ndi chikondi. Timakonda Mulungu ndiponso timafuna kumumvera. Timasangalala akamatiumba chifukwa timadziwa kuti malamulo ake si olemetsa. Mzimu woyera umatipatsanso mphamvu kuti tisaumbidwe ndi dzikoli komanso mzimu wake woipa. (Aef. 2:2) Paulo ali mnyamata anatengera mtima wonyada wa atsogoleri achiyuda. Koma atakhala mtumwi analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Nafenso tiyeni tizipempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera ndipo iye adzayankha mapemphero athuwo.—Sal. 10:17. w16.06 1:12
Lamlungu, October 7
Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu.—Chiv. 4:11.
Kuti Yehova akhale Mulungu wathu mmodzi yekha, m’pofunika kumalambira iye yekha basi. Anthu amene amalambira Yehova sayenera kukhulupiriranso maganizo kapena miyambo yabodza. Tiyenera kukumbukira kuti iye yekha ndiye Mulungu woona komanso wamphamvu amene tiyenera kumulambira. Kuti tizilambira Yehova yekha, tiyenera kusamala kuti tisalole chinthu chilichonse kulowa m’malo mwa iye. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kulambira Yehova yekha? Pa Malamulo Khumi aja, panali lamulo loti Aisiraeli asamalambire mafano kapena milungu ina. (Deut. 5:6-10) Masiku ano, kulambira mafano kungachitike m’njira zosiyanasiyana ndipo njira zina n’zovuta kuzizindikira. Koma zimene Yehova amafuna sizinasinthe ndipo iye adakali “Yehova mmodzi.”—Maliko 12:29. w16.06 3:10, 12
Lolemba, October 8
Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani.—Mat. 6:14.
Petulo atafunsa ngati tiyenera kukhululuka maulendo 7, Yesu ananena kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, mpaka nthawi 77.” Apa Yesu ankatanthauza kuti tiyenera kukhala ndi mtima wokhululuka nthawi zonse. (Mat. 6:15; 18:21, 22). Tizikumbukiranso kuti tonsefe tingalakwitse zinazake ndipo tingathe kukhumudwitsa ena. Choncho tikazindikira kuti takhumudwitsa munthu wina, tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo oti tizipita kwa munthuyo n’kukakambirana naye. (Mat. 5:23, 24) Timasangalala anthu ena akatikhululukira, choncho nafenso tizichita chimodzimodzi ngati anthu ena atikhumudwitsa. (1 Akor. 13:5; Akol. 3:13) Ndipotu Yehova amatikhululukira ngati nafenso timakonda kukhululukira ena. Choncho ena akatilakwira tizitsanzira Atate wathu wachifundo amene amatikhululukira.—Sal. 103:12-14. w16.06 4:15, 17
Lachiwiri, October 9
Pakuti sindichita nawo manyazi uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndi mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro.—Aroma 1:16.
M’masiku otsiriza ano anthu a Yehovafe talamulidwa kuti tizilalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu padziko lonse lapansi kumene kuli anthu kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mat. 24:14) Uthenga wathuwu tingatinso ndi “uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” Tikutero chifukwa choti madalitso onse amene tikuyembekezera kudzapeza Ufumuwu ukamadzalamulira, adzakhalapo chifukwa cha kukoma mtima kumene Yehova watisonyeza kudzera mwa Khristu. (Mac. 20:24; Aef. 1:3) Kodi ifeyo timatsanzira Paulo n’kumalalikira modzipereka posonyeza kuti timayamikira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu? (Aroma 1:14-15) Popeza ndife ochimwa, kukoma mtima kwa Yehova kukutithandiza m’njira zambiri. Choncho tili ndi udindo wothandiza anthu ena kuti adziwe mmene Yehova wawasonyezera chikondi komanso zimene angachite kuti apindule ndi zimenezo. w16.07 4:4, 5
Lachitatu, October 10
Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.”—Luka 12:40.
Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anachenjeza ophunzira ake katatu za “wolamulira wa dzikoli.” (Yoh. 12:31; 14:30; 16:11) Iye ankadziwa kuti Mdyerekezi adzachititsa anthu kuti akhale mumdima n’cholinga choti asakhale maso komanso asadziwe zimene zichitike posachedwapa. (Zef. 1:14) Satana amasocheretsa anthu pogwiritsira ntchito zipembedzo zonyenga. Kodi inuyo simuona umboni wakuti iye wachititsa “khungu maganizo a anthu osakhulupirira”? Ambiri sadziwa zoti Yesu akulamulira ndiponso zoti posachedwapa mapeto afika. (2 Akor. 4:3-6) Tikamalalikira timapeza anthu osafuna kumva uthenga wathu. Iwo amakayikira tikamawauza kuti mapeto ali pafupi. Tonsefe tikudziwa ubwino wokhala maso choncho tisalole kuti zochita za anthu ena zitifooketse kapena kutisokoneza. w16.07 2:11, 12
Lachinayi, October 11
Aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.—Aef. 5:33.
Pa tsiku la ukwati, aliyense amaoneratu kuti mwamuna ndi mkazi akusangalala kwambiri. Yehova ndi amene anayambitsa ukwati ndipo amafuna kuti mabanja azisangalala. Choncho iye wapereka malangizo anzeru m’Baibulo omwe angatithandize pa nkhaniyi. (Miy. 18:22) Koma Baibulo limanenanso mosabisa kuti popeza ndife ochimwa, tikalowa m’banja timakhala ndi “nsautso m’thupi.” (1 Akor. 7:28) Kodi tingachite chiyani kuti tichepetse mavutowa? Nanga Akhristu ayenera kuchita chiyani kuti banja lawo liziyenda bwino? Baibulo limasonyeza kuti chikondi n’chofunika kwambiri. M’Chigiriki muli mawu 4 ofotokoza mitundu yosiyanasiyana ya chikondi chomwe chimafunika m’banja. Mtundu woyamba (phi·liʹa) umanena za chikondi chimene munthu amasonyeza mnzake. Wachiwiri (eʹros) umanena za chikondi chapakati pa mwamuna ndi mkazi. Wachitatu (stor·geʹ) umanena za chikondi cha anthu apachibale ndipo chikondi chimenechi chimathandiza m’banja makamaka mukakhala ana. Ndipo womaliza (a·gaʹpe) umanena za chikondi chimene munthu amasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za makhalidwe abwino. Chikondi chimenechi n’chimene chimathandiza kwambiri kuti banja liziyenda bwino. w16.08 2:1, 2
Lachisanu, October 12
Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.
Pa nthawi imene Paulo ankalembera Timoteyo mawu amulemba la lerowa, Timoteyoyo ankadziwa kale kulalikira. Komabe kuti azilalikira mogwira mtima, anafunika kuti ‘nthawi zonse azisamala’ ndi zimene ankaphunzitsa. Sankafunika kuganiza kuti anthu azimvetserabe ngakhale atamangogwiritsa ntchito njira zimene anazolowera. Kuti apitirize kuwafika anthu pamtima, anayenera kukhala wokonzeka kusintha kuti ulaliki wake ugwirizane ndi munthu amene akumulalikira. Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Ofalitsa ena akamalalikira kunyumba ndi nyumba, sapeza anthu pakhomo. M’madera ena zimavuta kufika m’nyumba zina kapena kulowa m’mipanda. Ngati zoterezi zimachitikanso m’gawo lanu, mungachite bwino kupeza njira zina zolalikirira. Kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri kungathandize kuti anthu osiyanasiyana amve uthenga wabwino. Abale ndi alongo amene ayesapo njira imeneyi aona kuti ndi yothandiza kwambiri. Iwo amalalikira pamalo okwerera sitima ndi mabasi, m’misika, m’mapaki komanso malo ena opezeka anthu ambiri. w16.08 3:14-16
Loweruka, October 13
Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka.—Aheb. 12:12.
Yehova watipatsa abale padziko lonse amene angatilimbikitse. (Aheb. 12:12, 13) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani? Taganizirani zimene Aroni ndi Hura anachita pothandiza Mose kuti manja ake asagwe. (Eks. 17:8-13) Nafenso tiyenera kuyesetsa kuthandiza Akhristu amene akuvutika. Mwachitsanzo, tingathandize okalamba ndi odwala. Tingathandizenso amene akutsutsidwa ndi abale awo, akusowa ocheza nawo komanso omwe aferedwa. Ndi bwinonso kulimbikitsa achinyamata amene amakakamizidwa kuti achite zoipa, apeze chuma chambiri kapena aphunzire kwambiri n’cholinga choti adzapeze ntchito yapamwamba. (1 Ates. 3:1-3; 5:11, 14) Tiziyesetsanso kulimbikitsa anthu nthawi zonse kaya ndi ku Nyumba ya Ufumu, mu utumiki, tikamadya nawo kapena tikamacheza nawo pafoni. w16.09 1:13, 14
Lamlungu, October 14
Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.—1 Akor. 10:31.
Timalemekeza Mulungu wathu woyera, Akhristu anzathu komanso anthu amene timawalalikira. Choncho timayesetsa kuvala zovala zimene zingachititse kuti anthu alemekeze Yehova komanso zogwirizana ndi uthenga wathu. (Aroma 13:8-10) Timachita zimenezi makamaka tikamapita kukalalikira kapena kukasonkhana. Tiyenera kuvala ‘mogwirizana ndi mmene anthu amene amati amalemekeza Mulungu ayenera kuvalira.’ (1 Tim. 2:10) Komabe tikudziwa kuti zovala zimene zingakhale zoyenera pamalo ena, zingakhale zosayenera pamalo ena. Ndi bwinonso kuganizira chikhalidwe cha komwe tikukhala n’cholinga choti tisakhumudwitse ena. Tikamapita kumsonkhano wadera kapena wachigawo, tiyenera kuvala zovala zabwino osati zotengera masitayilo oipa a m’dzikoli. Komanso ngati tikugonera komweko, tikamacheza madzulo kapena m’mawa nthawi ya msonkhano isanakwane, tiyenera kuvala bwino osati motayirira. N’chimodzimodzinso ngati tikugonera kuhotelo. Tikatero sitichita manyazi kuuza anthu kuti ndife a Mboni komanso timatha kulalikira mpata ukapezeka. w16.09 3:7, 8
Lolemba, October 15
Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.—Aheb. 3:4.
Chitsanzo chimene Paulo ananenachi ndi chothandiza kwambiri. Tikaona chinthu chopangidwa mwaluso timadziwa kuti payenera kukhala winawake amene anachipanga. Mungathenso kugwiritsa ntchito njira yosavutayi pokambirana ndi anthu amene amakayikira kuti Baibulo ndi lolondola. Yesani kudziwa zimene amakhulupirira ndipo kenako pezani nkhani zimene zingawachititse chidwi. (Miy. 18:13) Ngati amakonda sayansi, mungakambirane nawo mfundo zosonyeza kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi. Ena angachite chidwi ndi mfundo zosonyeza kuti maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa komanso Baibulo ndi lolondola pa nkhani ya mbiri yakale. Njira inanso n’kuwasonyeza mfundo za m’Baibulo zothandiza ngati zimene zimapezeka mu ulaliki wa Yesu wapaphiri. Musaiwale kuti cholinga chanu ndi kuwafika pamtima osati kuwina mkangano. Choncho akamalankhula muzimvetsera. Muzifunsa mafunso abwino komanso muzilankhula mokoma mtima ndi mwaulemu, makamaka mukamalankhula ndi achikulire. Mukatero nawonso angamvetsere zimene mukunena. w16.09 4:14-16
Lachiwiri, October 16
Landiranani.—Aroma 15:7.
Kuti tithandize alendo kukhala omasuka, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikanakhala m’dziko lachilendo, ndikanafuna kuti anthu andichitire zotani?’ (Mat. 7:12) Muzikhala oleza mtima ndi anthu amene akuvutikabe kuzolowera moyo watsopano. Poyamba tingamavutike kumvetsa maganizo ndiponso zochita za anthu achilendowo. M’malo moyembekezera kuti iwo asinthe tiyenera kungololera kuti azichita zinthu mogwirizana ndi chikhalidwe chawo. Tikadziwa zinthu zina zokhudza chikhalidwe cha alendowo komanso kumene anachokera, tikhoza kupeza zolankhula pocheza nawo. Mwina pa nthawi ya kulambira kwa pabanja tingafufuze za anthu achilendo mumpingo wathu kapena m’gawo lathu. Kuwaitana kuti adzadye nafe chakudya kumathandizanso kuti tizigwirizana nawo. Popeza Yehova “anatsegulira anthu a mitundu ina khomo lolowera m’chikhulupiriro,” nafenso tiyenera kuitanira kunyumba kwathu alendo amene ndi “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.”—Mac. 14:27; Agal. 6:10; Yobu 31:32. w16.10 1:15, 16
Lachitatu, October 17
Ganizirani mozama za munthu amene anapirira malankhulidwe onyoza ngati amenewo a anthu ochimwa.—Aheb. 12:3.
Paulo atafotokoza za anthu amene anali ndi chikhulupiriro, anatchula za Yesu Khristu yemwe ndi chitsanzo choposa onse. Lemba la Aheberi 12:2 limati: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo. Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” Tiyenera ‘kuganizira mozama’ chitsanzo cha Yesu chifukwa anakhalabe wokhulupirika atakumana ndi mayesero aakulu kwambiri. Akhristu enanso oyambirira monga Antipa anaphedwa chifukwa chakuti anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu. (Chiv. 2:13) Mosiyana ndi anthu akale okhulupirika, Akhristu amenewa analandira kale mphoto. (Aheb. 11:35) Patangopita nthawi kuchokera pamene Yesu anakhala Mfumu mu 1914, Akhristu odzozedwa amene anali atamwalira anaukitsidwa n’kupita kumwamba kuti akalamulire limodzi ndi Yesu.—Chiv. 20:4. w16.10 3:12
Lachinayi, October 18
Pitirizani kudandaulirana [kulimbikitsana] tsiku ndi tsiku.—Aheb. 3:13.
Makolo ena sayamikira ana awo chifukwa choti makolo awo sankawalimbikitsa. Komanso ogwira ntchito ambiri sayamikiridwa choncho amadandaula kuti palibe amene amawalimbikitsa akakhala kuntchito. Nthawi zambiri tikamalimbikitsa munthu timamuyamikira chifukwa cha zinthu zabwino zimene wachita. Timathanso kumuuza za makhalidwe abwino amene ali nawo. Tikhozanso ‘kulankhula mawu olimbikitsa’ kwa anthu amene afooka kapena akhumudwa ndi zinazake. (1 Ates. 5:14) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kulimbikitsa” amatanthauza “kuitana munthu kuti akhale nawe pafupi.” Nthawi zonse tiziyesetsa kupeza mpata wouza abale ndi alongo athu mawu olimbikitsa. (Mlal. 4:9, 10) Kodi timagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka n’kuthandiza ena kudziwa chifukwa chake timawakonda komanso kuwayamikira? Tingathe kuchita zimenezi ngati timaganizira kwambiri mwambi wakuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.”—Miy. 15:23. w16.11 1:3-5
Lachisanu, October 19
Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!—Sal. 133:1.
Yehova analoseranso za anthu ake kuti: “Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola.” (Mika 2:12) Iye anauziranso Zefaniya kulosera kuti: “Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera [kutanthauza choonadi cha m’Malemba] kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.” (Zef. 3:9) Ndi mwayi waukulu kulambira Yehova mogwirizana. Apa zikuonekeratu kuti malangizo a m’Malemba anathandiza mpingo wa ku Korinto komanso mipingo ina kuti ikhale yoyera, yamtendere komanso yogwirizana. (1 Akor. 1:10; Aef. 4:11-13; 1 Pet. 3:8) Masiku anonso, anthu a Mulungu ndi ogwirizana ndipo izi zikuchititsa kuti azitha kulalikira uthenga wabwino padziko lonse. w16.11 2:16, 18
Loweruka, October 20
Inu ndinu . . . “ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri” a amene anakuitanani kuchoka mu mdima.—1 Pet. 2:9.
Kwa zaka mahandiredi angapo kuchokera pamene Yesu anaphedwa, anthu ambiri ankawerenga Baibulo m’Chigiriki kapena Chilatini. Choncho ankatha kusiyanitsa zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zimene zinkaphunzitsidwa kutchalitchi. Zimene ankawerengazo zinachititsa kuti ayambe kukayikira zimene matchalitchi ankaphunzitsa. Komabe zinali zovuta kuti anene poyera maganizo awo chifukwa zikanachititsa kuti azunzidwe kapena kuphedwa. Patapita nthawi, anthu olankhula Chigiriki ndi Chilatini anayamba kuchepa. Koma atsogoleri a tchalitchi sankalola kuti Mawu a Mulungu amasuliridwe m’zilankhulo zimene anthu ambiri ankalankhula. Izi zinachititsa kuti Baibulo lizingowerengedwa ndi atsogoleri achipembedzo kapena anthu ena ophunzira. Zinkatero ngakhale kuti ena mwa atsogoleri achipembedzowo sankadziwa bwino kuwerenga ndi kulemba. Munthu aliyense wotsutsa zimene tchalitchi chinkaphunzitsa ankalangidwa koopsa. Pa nthawiyi, odzozedwa okhulupirika ankangosonkhana m’timagulu ting’onoting’ono ndipo ena sankasonkhana n’komwe. Mofanana ndi Ayuda amene anali ku Babulo, tingati ‘ansembe achifumuwa’ sankagwira ntchito yawo bwinobwino. Apatu Akhristu oona anali opanikizika mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. w16.11 4:8, 10, 11
Lamlungu, October 21
Anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.—1 Akor. 6:9.
Tiyenera kupewa machimo akuluakulu ngati amene ankachitika ku Korinto. Zimenezi n’zofunika kwambiri ngati tikufuna kusonyeza kuti timayamikira kukoma mtima kwa Mulungu ndipo ‘uchimo sukutilamulira.’ Koma funso limene tiyenera kudzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi ndimayesetsa “kumvera mochokera pansi pa mtima” popewanso machimo ooneka ngati ang’onoang’ono?’(Aroma 6:14, 17) Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Tikudziwa kuti iye sankachita zoipa ngati zimene zatchulidwa pa 1 Akorinto 6:9-11. Koma iye anavomereza kuti anali wochimwa. Paja analemba kuti: “Ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo. Sindimvetsetsa kuti n’chifukwa chiyani ndimachita zinthu motere. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita.” (Aroma 7:14, 15) Mawuwa akusonyeza kuti pali zinthu zina zimene Paulo ankachita zomwe ankaona kuti ndi machimo ndipo ankayesetsa kuti asiye. (Aroma 7:21-23) Ifenso tiyenera kukhala ndi maganizowa tikamayesetsa kumvera Mulungu “mochokera pansi pa mtima.” w16.12 1:15, 16
Lolemba, October 22
Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.—Sal. 55:22.
Tikakhala ndi nkhawa tiyenera kufotokozera Atate wathu wakumwamba. Mukakhala ndi malingaliro osautsa, n’kuchita zonse zomwe mungathe polimbana ndi vuto lanu, pemphero lochokera pansi pamtima lingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri. (Sal. 94:18, 19) Lemba la Afilipi 4:6, 7 limasonyeza kuti Yehova angayankhe pemphero lathu lochonderera komanso lochokera pansi pa mtima. Koma kodi angayankhe bwanji? Angatipatse mtendere wamumtima umene ungatithandize kuti tisiye kuda nkhawa kwambiri. Anthu ambiri angavomereze kuti zoterezi zinawachitikirapo. Pamene anali ndi nkhawa komanso mantha Yehova anawathandiza kukhala ndi mtendere wamumtima umene umaposa kuganiza mozama kulikonse. Zoterezi zikhoza kukuchitikiraninso inuyo. Ngati muli ndi vuto linalake, “mtendere wa Mulungu” ungakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri. Muzikhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—Yes. 41:10. w16.12 3:3, 4
Lachiwiri, October 23
Mwa chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.—Aheb. 11:24.
Mose anasiya chuma cha ku Iguputo ndipo “anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” (Aheb. 11:25, 26) Tiyeni tizitsanzira chikhulupiriro cha anthu akale monga Mose, ndipo tizigwiritsa ntchito moyenera ufulu wathu wosankha, pochita chifuniro cha Mulungu. Anthu ena amaona kuti zimakhala zophweka kuti wina azingowasankhira zochita. Koma tikamachita zimenezi tingalephere kugwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha, womwe ndi mphatso ya mtengo wapatali, posankha zinthu zofunika kwambiri. Zinthu zake zafotokozedwa palemba la Deuteronomo 30:19, 20. Vesi 19 likusonyeza kuti Mulungu anapatsa Aisiraeli ufulu woti asankhe zimene ankafuna kuchita. Pamene vesi 20 likusonyeza kuti Yehova anawapatsa mwayi woti asonyeze zimene zinali mumtima mwawo. Ifenso tingasankhe kuti tizilambira Yehova. Tingathenso kusankha kuti tizigwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha potamanda Yehova komanso posonyeza zimene zili mumtima mwathu. w17.01 2:10, 11
Lachitatu, October 24
Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino . . . ndipo khala wokhulupirika m’zochita zako zonse.—Sal. 37:3.
Yehova amafuna kuti tizigwiritsa ntchito bwino luso limene anatipatsa. Zili choncho chifukwa iye amatikonda komanso amadziwa kuti tikagwiritsa ntchito bwino luso limeneli timasangalala. Koma Yehova amadziwanso kuti pali zinthu zina zimene sitingathe kuchita. Mwachitsanzo, patokha sitingakhale angwiro, sitingachotse uchimo ndipo sitingathetse imfa. Sitingaletsenso anthu ena kuchita zinthu zina chifukwa nawonso ali ndi ufulu wosankha. (1 Maf. 8:46) Ndipo ngakhale titadziwa zinthu zambiri bwanji, timakhalabe ngati ana pamaso pa Yehova. (Yes. 55:9) Choncho tiyenera kudalira Yehova n’kumamulola kuti azititsogolera chifukwa akhoza kutichitira zinthu zimene sitingakwanitse. Komabe tiyenera kuchita zimene tingathe kuti tithane ndi mavuto athu komanso tithandize anzathu. Mwachidule tingati tiyenera ‘kukhulupirira Yehova, ndi kuchita zabwino.’ w17.01 1:2-4
Lachinayi, October 25
Tiye tiwolokere ku Yerusalemu ndipo tizikadya chakudya pamodzi.—2 Sam. 19:33.
Barizilai anakana zimene Davide anamuuzazi poona kuti anali wokalamba ndipo sanafune kuti akakhale mtolo kwa Davide. Choncho anauza Davide kuti atenge Chimamu, yemwe mwina anali mwana wake. (2 Sam. 19:31-37) Kudzichepetsa n’kumene kunathandiza Barizilai kuti asankhe bwino pa nkhaniyi. Sikuti iye anakana kupita ndi Davide chifukwa choti ankaona kuti ndi udindo woti sangaukwanitse. Si chifukwanso choti ankafuna moyo waphee osati wakunyumba yachifumu. Koma ndi chifukwa choti ankadziwa kuti zinthu zinali zitasintha pa moyo wake chifukwa cha ukalamba. Ankadziwanso kuti sakanatha kuchita zinthu zina choncho anaona kuti si bwino kudzikakamiza. (Agal. 6:4, 5) Ifenso tiyenera kukhala odzichepetsa. Tisamadziyerekezere ndi ena komanso tisamangoganizira za udindo kapena kutchuka. Koma tizingoyesetsa kuchita zimene tingathe potumikira Yehova. (Agal. 5:26) Kudzichepetsa kungatithandize kuti tizigwira ntchito limodzi ndi abale athu polemekeza Yehova komanso kuthandiza ena.—1 Akor. 10:31. w17.01 4:5, 6
Lachisanu, October 26
Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.—Gen. 1:31.
Yehova ndi Mlengi wodabwitsa. Zinthu zonse zimene analenga n’zokongola komanso zapamwamba kwambiri. (Yer. 10:12) Yehova anakhazikitsa malamulo a chilengedwe komanso malamulo a makhalidwe abwino n’cholinga choti zinthu zonse zizichitika mwadongosolo. (Sal. 19:7-9) Chilichonse m’chilengedwechi anachiika pamalo ake ndipo chimagwira ntchito yake mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, mphamvu imene imachititsa kuti dziko likhazikike m’malere imathandizanso kuti madzi a m’nyanja asasefukire. Izi zimathandiza kuti padzikoli pakhale bata komanso kuti zamoyo zizisangalala. Anthu kuphatikizapo zolengedwa zonse zimatsatira malamulo amene Mulungu anakhazikitsawa. Zonsezi zimasonyeza kuti Mulungu ali nalo cholinga dzikoli komanso anthu. Choncho tikakhala mu utumiki, tingachite bwino kumafotokozera anthu za Mulungu amene amachititsa kuti zinthu zizichitika mwadongosolo chonchi.—Chiv. 4:11. w17.02 1:4, 5
Loweruka, October 27
Mose . . . ndi amene Mulungu anamutumiza monga wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo.—Mac. 7:35.
Mose atafa, “kalonga wa gulu lankhondo la Yehova” anathandiza Yoswa kuti atsogolere Aisiraeli pogonjetsa Akanani. (Yos. 5:13-15; 6:2, 21) Pa nthawi ya Mfumu Hezekiya, gulu la asilikali a Asuri linaopseza kuti liwononga Yerusalemu. Koma usiku umodzi wokha, “mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.” (2 Maf. 19:35) Angelo ndi angwiro koma anthu amene ankathandizidwa ndi angelowo ankalakwitsa zinthu zina. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Mose analephera kulemekeza Mulungu. (Num. 20:12) Nayenso Yoswa anaiwala kufunsa kaye Mulungu asanachite pangano ndi anthu a ku Gibeoni. (Yos. 9:14, 15) Ponena za Hezekiya, Baibulo limati pa nthawi ina “mtima wake unayamba kudzikuza.” (2 Mbiri 32:25, 26) Koma ngakhale kuti anthuwa ankalakwitsa zina ndi zina, Aisiraeli ankayenerabe kuwamvera. Tikutero chifukwa choti Yehova ankatuma angelo kuti aziwathandiza. Choncho mwachidule tingati Yehovayo ndi amene ankatsogolera anthu ake. w17.02 3:7-9
Lamlungu, October 28
Iye wokhala pampando wachifumu, ndi Mwanawankhosa, atamandidwe ndiponso alandire ulemu, ulemerero, ndi mphamvu, kwamuyaya.—Chiv. 5:13.
Kupereka ulemu kwa munthu kumatanthauza kuchita zinthu zosonyeza kuti timamulemekeza. Nthawi zambiri munthu woyenera kulemekezedwayo amakhala kuti wachita zinazake kapena ali ndi udindo winawake. Ndiye tingafunse kuti, kodi tiyenera kupereka ulemu kwa ndani, ndipo n’chifukwa chiyani? Lemba la Chivumbulutso 5:13 limasonyeza kuti ‘wokhala pampando wachifumu ndiponso Mwanawankhosa’ ayenera kulemekezedwa. Chaputala 4 cha buku lomweli chimafotokoza chifukwa chake Yehova ali woyenera kupatsidwa ulemu. Angelo amatamanda mokweza Yehova “amene adzakhalabe ndi moyo kwamuyaya.” Iwo amati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”—Chiv. 4:9-11. w17.03 1:1, 2
Lolemba, October 29
Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa.—Miy. 28:26.
Anthu ambiri akafuna kusankha zochita amangotsatira zimene mtima wawo ukufuna. Komatu kuchita zimenezi n’koopsa ndiponso n’kosemphana ndi mfundo za m’Malemba. Baibulo limatichenjeza kuti tikafuna kusankha zochita tisamangotsatira zofuna za mtima wathu. Limafotokozanso kuti pamakhala zotsatira zomvetsa chisoni tikamangotsatira zofuna za mtima wathu. Sitingadalire mtima wathu chifukwa “ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yer. 3:17; 13:10; 17:9; 1 Maf. 11:9) Ndiye kodi mukuganiza kuti zinthu zingakuthereni bwanji mutati muzingotsatira mtima wanu posankha zochita? Mwachitsanzo, kodi chingachitike n’chiyani ngati tingasankhe zochita titakwiya? Yankho la funsoli n’lodziwikiratu. (Miy. 14:17; 29:22) Komanso ngati tikusankha zochita titakhumudwa, kodi tingasankhe mwanzeru? (Num. 32:6-12; Miy. 24:10) N’zoonekeratu kuti sitiyenera kusankha zochita titakwiya kapena titakhumudwa. w17.03 2:12, 13
Lachiwiri, October 30
Ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu.—2 Maf. 20:3.
Popeza anthufe si ife angwiro, timalakwitsa zambiri. Koma tikuthokoza Yehova chifukwa anatipatsa dipo ndipo ndi wokonzeka kutikhululukira. Choncho tikadzichepetsa n’kulapa, tingathe kumupempha kuti atikhululukire. Timayamikira kuti iye ‘satichitira mogwirizana ndi machimo athu.’ (Sal. 103:10) Komabe, mogwirizana ndi zimene Davide anauza Solomo, tiyenera kutumikira Yehova “ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 28:9) Zimenezi n’zofunika kuti Yehova azisangalala ndi zimene timachita pomulambira. Koma kodi anthu ochimwafe tingachite bwanji zimenezi? Munthu amene amatumikira Yehova ndi “mtima wathunthu” amakonda kwambiri Yehova ndipo amafuna kumulambira mpaka kalekale. M’Baibulo mawu akuti “mtima” nthawi zambiri amanena za munthu wamkati. Amanena za mmene munthu amaganizira, zimene amakonda, zimene amafuna kuchita pa moyo wake komanso zolinga zake pochita zinthu. Munthu amene amatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu sachita zinthu mwachinyengo kapena mwamwambo. Choncho ngakhale kuti si ife angwiro, ngati tili odzipereka kwambiri komanso timapewa chinyengo, tingathe kumatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu.—2 Mbiri 19:9. w17.03 3:1, 3
Lachitatu, October 31
[Yehova] amaona wodzichepetsa, koma wodzikuza samuyandikira.—Sal. 138:6.
Kodi ifeyo timatani ngati tachita zinazake zabwino ndipo anthu ena akutiyamikira? Zimene tingachite, zingasonyeze zomwe zili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, m’bale wina angakambe bwino nkhani yake pamsonkhano ndipo anthu ambiri angamuyamikire. Kodi pamenepa angatani? Anthu akatiyamikira pa zabwino zomwe tachita, tiyenera kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’” (Luka 17:10) Ndiye kodi tingatani kuti tisachite zinthu ngati Hezekiya? Paja Hezekiya atadzikuza, anasonyeza kuti sanayamikire zimene Yehova anamuchitira. (2 Mbiri 32:24-27, 31) Tikamaganizira kwambiri zimene Mulungu watichitira, tingapewe mtima wonyada umene iye amadana nawo. M’malomwake tingamalankhule zinthu zosonyeza kuti timayamikira Yehova, yemwe amathandiza anthu ake nthawi zonse. w17.03 4:12-14