Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es18 tsamba 108-118
  • November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2018
  • Timitu
  • Lachinayi, November 1
  • Lachisanu, November 2
  • Loweruka, November 3
  • Lamlungu, November 4
  • Lolemba, November 5
  • Lachiwiri, November 6
  • Lachitatu, November 7
  • Lachinayi, November 8
  • Lachisanu, November 9
  • Loweruka, November 10
  • Lamlungu, November 11
  • Lolemba, November 12
  • Lachiwiri, November 13
  • Lachitatu, November 14
  • Lachinayi, November 15
  • Lachisanu, November 16
  • Loweruka, November 17
  • Lamlungu, November 18
  • Lolemba, November 19
  • Lachiwiri, November 20
  • Lachitatu, November 21
  • Lachinayi, November 22
  • Lachisanu, November 23
  • Loweruka, November 24
  • Lamlungu, November 25
  • Lolemba, November 26
  • Lachiwiri, November 27
  • Lachitatu, November 28
  • Lachinayi, November 29
  • Lachisanu, November 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2018
es18 tsamba 108-118

November

Lachinayi, November 1

Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.​—Miy. 27:11.

Satana amaona kuti palibe munthu amene amatumikira Yehova chifukwa chomukonda. (Yobu 2:4, 5) Maganizo amenewa adakali nawobe mpaka pano. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi imene anathamangitsidwa kumwamba n’kuti akupitirizabe kuneneza atumiki a Mulungu okhulupirika “usana ndi usiku.” (Chiv. 12:10) Choncho Satana amaonabe kuti anthufe sitingakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati titakumana ndi mavuto. Amafunitsitsa kutiona titasiya kumvera Yehova ndiponso kumutumikira. Choncho mukakumana ndi mavuto muziyerekezera kuti mukuona magulu awiri. Mbali ina kuli Satana ndi ziwanda zake ndipo akunena kuti mavutowo akakupanikizani musiya kutumikira Yehova. Mbali ina kuli Yehova, Yesu, angelo ndiponso odzozedwa amene anaukitsidwa ndipo onse akukuchemererani. Iwo akusangalala chifukwa choti mukuyesetsa kupirira ndipo mukusonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Ndiyeno mukumva Yehovayo akukuuzani mawu amulemba la lerowa. w16.04 2:8, 9

Lachisanu, November 2

Upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri.​—Mat. 18:16.

Munthu amene mwapita kukalankhula naye akavomereza kulakwa kwake, ndiye kuti ‘mwabweza m’bale wanuyo.’ Muyenera kupititsa nkhaniyo kwa akulu pokhapokha ngati mwachita zonse zotchulidwa pa Mateyu 18:15-17, koma sizinathandize. Si nthawi zambiri pamene nkhani zoterezi zimafika poti munthu n’kuchotsedwa. Nkhani zambiri zimatha anthu atangokambirana pa awiri kapena ndi mboni zina. Nthawi zambiri munthu amazindikira kulakwa kwake n’kusintha. Zikatere wolakwiridwayo amaona kuti palibenso chifukwa choikokera nkhaniyo. Choncho si bwino kufulumira kuuza akulu nkhani yoti simunakambirane. Akulu amasamalira nkhaniyo pokhapokha ngati mwatsatira kale mfundo ziwiri zija komanso ngati pali umboni wosonyeza kuti nkhaniyo inachitikadi. w16.05 1:15, 16

Loweruka, November 3

Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.—Yoh. 17:16.

Timapewa ndale chifukwa chakuti timafuna kukhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu. Kodi zingakhale zomveka kuti tizilalikira zoti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto, uku tikuthandizira andale? Anthu a m’zipembedzo zonyenga amagawanika chifukwa cha ndale. Koma Akhristu oona amakhala ogwirizana chifukwa salola kuti ndale ziwagawanitse. (1 Pet. 2:17) Tiyenera kudziwa kuti pamene mapeto akuyandikira, tikhoza kukumana ndi mayesero pa nkhaniyi. M’dzikoli, anthu ambiri ndi “osafuna kugwirizana ndi anzawo” komanso “osamva za ena.” Choncho m’posavuta kuti anthu akhale ogawanika. (2 Tim. 3:3, 4) M’mayiko ena, zinthu zikasintha chifukwa cha ndale, abale ndi alongo amakumana ndi mavuto osayembekezereka. Choncho tiyenera kukonzekera panopa kuti tisakhale mbali ya dzikoli. Tikutero chifukwa chakuti tikangokhala mpaka pamene mayeserowo afika, tikhoza kugonja. w16.04 4:3, 4

Lamlungu, November 4

Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.—Agal. 6:7.

Anthu ena angaganize kuti palibe vuto ndi zimene amasankha kuchita. Koma kuti tikondweretse Yehova, tiyenera kuganizira malamulo komanso mfundo zopezeka m’Mawu ake n’kusankha mogwirizana ndi zimenezo. Mwachitsanzo, kuti Mulungu azisangalala nafe tiyenera kutsatira lamulo lake pa nkhani ya magazi. (Gen. 9:4; Mac. 15:28, 29) Tingamupemphe kuti atithandize kuti tizisankha zochita mogwirizana ndi malamulo komanso mfundo za m’Malemba. Zimene timasankha pa nkhani zikuluzikulu zingalimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova kapena kuuwononga. Komanso zosankha zolakwika zingafooketse chikhulupiriro cha ena, kuwakhumudwitsa ndiponso zingasokoneze mtendere mumpingo. Choncho kusankha zochita mwanzeru n’kofunika kwambiri.​—Aroma 14:19. w16.05 3:4, 5

Lolemba, November 5

Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.—Yes. 48:17.

Yehova amayamikira kwambiri tikamayesetsa ‘kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’ powerenga Baibulo nthawi zonse komanso kuphunzira patokha. (Aef. 5:15, 16) N’zoona kuti sizophweka kuwerenga mwatsatanetsatane chilichonse chimene tingalandire. Komabe m’pofunika kusamala pa nkhani imeneyi. Tiyenera kusamala kuti tisamalephere kuphunzira zinthu zina poganiza kuti mfundo zake sizikutikhudza. Mwachitsanzo, kodi munaganizapo kuti nkhani inayake ya m’Baibulo sikukukhudzani inuyo? Nanga mumatani mukaona kuti nkhani ina ya m’magazini kapena m’buku alembera gulu linalake la anthu? Kodi mumangoiwerenga patalipatali mwinanso osaiwerenga n’komwe? Ngati timachita zimenezi ndiye kuti sitingapindule. Ndiye kodi tingatani kuti zoterezi zisamatichitikire? M’pofunika kuti tizikumbukira kuti zinthu zimene timalandira ndi zochokera kwa Yehova. w16.05 5:5, 6

Lachiwiri, November 6

Ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu, yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.​—Agal. 6:1.

Yehova amagwiritsa ntchito mpingo wachikhristu komanso akulu kuti atiumbe. Mwachitsanzo, akulu akazindikira kuti tili ndi mavuto enaake, amayesetsa kutithandiza koma sadalira nzeru zawo. Iwo modzichepetsa amapempha Yehova kuti awathandize kukhala anzeru komanso ozindikira. Kenako amafufuza m’Mawu a Mulungu komanso m’mabuku athu. Zimenezi zimawathandiza kuti adziwe mmene angatithandizire. Kumvetsa mmene Mulungu amatiumbira kumatithandiza kuti tiziona moyenera Akhristu anzathu komanso anthu a m’gawo lathu, kuphatikizapo amene timaphunzira nawo Baibulo. Mulungu satikakamiza kuti tisinthe koma amalemekeza ufulu wathu wosankha zochita ndipo amatilola kuti tichotse kaye tokha timakhalidwe tosafunika. Kuti tithe kuchita zimenezi amatithandiza kuzindikira mfundo zake zolungama. w16.06 1:13, 14

Lachitatu, November 7

Ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna.​—Yer. 45:5.

Mtumwi Yohane ananena kuti ngati munthu akukonda zinthu za m’dziko “ndiye kuti sakonda Atate.” Zina mwa zinthu za m’dzikozi ndi monga “chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:15, 16) Choncho tiyenera kudzifufuza nthawi zonse kuti tione ngati tayamba kukonda zinthu za m’dziko pa nkhani ya zosangalatsa, anthu ocheza nawo ndiponso mafashoni. Komanso kukonda zinthu za m’dziko kungachititse munthu kufuna “zinthu zazikulu,” mwina kudzera m’maphunziro apamwamba. Panopa, tatsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano. Choncho ndi bwino kuti tizikumbukira mawu a Mose a pa Deuteronomo 6:4 akuti “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi,” ndipo tiziyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe kuti tizimutumikira m’njira imene amavomereza.​—Aheb. 12:28, 29. w16.06 3:14

Lachinayi, November 8

Koma inu, pitirizani kufunafuna ufumu [wa Mulungu], ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.—Luka 12:31.

Zofunika pa moyo wathu n’zochepa koma zimene timalakalaka titakhala nazo ndi zambiri. Vuto ndi lakuti anthu ambiri satha kusiyanitsa zinthu zofunika pa moyo ndi zosafunika kwenikweni. Kodi kusiyana kwake kuli pati? “Zofunika pa moyo” ndi zinthu zimene titapanda kukhala nazo sitingakhale ndi moyo. Apa tikunena chakudya, zovala ndi malo ogona. Koma “zinthu zosafunika kwenikweni” ndi zimene tikhoza kukhala ndi moyo ngakhale tilibe. Zinthu zosafunika kwenikweni zimene anthu amazilakalaka zimasiyana malinga ndi kumene anthuwo akukhala. M’mayiko osauka, ambiri amafuna atakhala ndi foni, njinga yamoto kapena malo. Koma m’mayiko olemera anthu amafuna atakhala ndi zovala zapamwamba, nyumba yaikulu komanso galimoto yodula. Koma msampha wokonda chuma umakhudza anthu m’dziko lililonse. Anthu amachita chilichonse chimene angathe kuti apeze zomwe akufuna ngakhale zitakhala zosafunika kwenikweni komanso zodula kwambiri.​—Aheb. 13:5. w16.07 1:1-3

Lachisanu, November 9

Musamakonzekere kuchita zilakolako za thupi.​—Aroma 13:14.

Masiku ano anthu akutanganidwa kwambiri ndi zinthu zina moti sazindikira “zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Iwo amakopeka ndi zinthu za m’dzikoli zimene zimalimbikitsa ‘chilakolako cha thupi ndi cha maso.’ (1 Yoh. 2:16) Timayesetsa kupewa mzimu wa dziko ndipo timafuna kuti mzimu wa Mulungu uzititsogolera. Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wakewu potithandiza kumvetsa zinthu zimene zichitike posachedwapa. (1 Akor. 2:12) Komabe timadziwa kuti kupanda kusamala, ngakhale zinthu zabwinobwino zingatilepheretse kukhala maso. (Luka 21:34, 35) Anthu ena angamatinyoze akaona kuti tikuyesetsa kukhala maso, koma tisalole kuti zimenezi zitifooketse. (2 Pet. 3:3-7) M’malomwake tiyenera kusonkhana ndi Akhristu anzathu chifukwa mzimu wa Mulungu umapezeka kumisonkhanoko. w16.07 2:13, 14

Loweruka, November 10

Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu. . . . Inu mudzatikhululukira machimo athu.​—Sal. 65:2, 3.

Anthu ambiri amangopemphera chifukwa amaona kuti akapemphera mtima wawo umakhala m’malo. Koma sakhulupirira kuti Mulungu amamva mapemphero awo. Anthu oterewa tiyenera kuwathandiza kudziwa kuti Yehova ndi “Wakumva pemphero.” Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati mutapempha chilichonse m’dzina langa, ine ndidzachichita.” (Yoh. 14:14) Mawu akuti “chilichonse” akunena za chilichonse chogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. Yohane anati: “Timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yoh. 5:14) Tiyenera kuphunzitsa anthu kuti adziwe kuti pemphero silimangothandiza kuti maganizo a munthu akhale m’malo. Koma lingatithandize kuti tiyandikire “mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu” wa Yehova. (Aheb. 4:16) Tikawaphunzitsa kuti azipemphera kwa Yehova, moyenera komanso azipempha zinthu zoyenera, tingawathandize kuti akhale naye pa ubwenzi ndiponso azilimbikitsidwa pa nthawi ya mavuto.​—Sal. 4:1; 145:18. w16.07 4:11, 12

Lamlungu, November 11

Okhulupirika anu adzakutamandani. Iwo adzanena za ulemerero wa ufumu wanu. Ndi kulankhula za mphamvu zanu, kuti ana a anthu adziwe ulemerero wa ufumu wanu.​—Sal. 145:10-12.

Mawu amenewa akufotokoza bwino mmene abale ndi alongo ambiri amamvera. Koma bwanji ngati simutha kuchita zambiri potumikira Yehova chifukwa cha matenda, ukalamba kapena mavuto ena? Muzikumbukira kuti mukamalalikira anthu ena, monga amene akukusamalirani, ndiye kuti mukuchita utumiki wopatulika umene umalemekeza Mulungu. Ngati muli m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chanu, muyenera kuti nthawi zina mumapeza mpata wolalikira ndipo zimenezi zimasangalatsa Yehova. (Miy. 27:11) N’chimodzimodzinso kwa anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti ali m’banja limene wina si Mboni. (1 Pet. 3:1-4) Zimenezi zikusonyeza kuti aliyense angathe kutamanda Yehova komanso kuchita zambiri pomutumikira ngakhale patakhala mavuto. Yehova adzakudalitsani mukamayesetsa kulalikira uthenga wabwino kwa anthu amene alibe chiyembekezo. w16.08 3:19, 20

Lolemba, November 12

Akazi agonjere amuna awo ngati mmene amagonjerera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo.—Aef. 5:22, 23.

Mawu amenewa sakusonyeza kuti mkazi ndi wotsika poyerekezera ndi mwamuna. Koma amangothandiza kuti mkaziyo azikwaniritsa udindo umene Mulungu anamupatsa. Paja Yehova anati: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” (Gen. 2:18) Khristu yemwe ndi “mutu wa mpingo” amakonda kwambiri mpingowo. Amuna achikhristu nawonso ayenera kukonda mabanja awo. Akamachita zimenezi, akazi awo amadzimva kuti ndi otetezeka ndipo zimakhala zosavuta kuti azilemekeza, kuthandiza komanso kugonjera amuna awowo. Tiyenera kutsanzira Yesu n’kumakondana ngati mmene iye ankakondera ophunzira ake. (Yoh. 13:34, 35; 15:12, 13; Aef. 5:2) Choncho anthu okwatirana ayenera kukondana kwambiri moti aliyense azikhala wokonzeka kufera mnzake ngati patafunika kutero. w16.08 2:3, 4

Lachiwiri, November 13

Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.—Miy. 15:23.

Nafenso mawu athu akhoza kulimbikitsa anthu ena kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Tisaiwalenso kuti tikapereka ndemanga zabwino pamisonkhano timalimbikitsa kwambiri anthu ena. Yehova anathandiza Nehemiya ndi anzake kuti alimbitse manja awo n’kumaliza ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. Ntchitoyi inatha patangodutsa masiku 52 okha. (Neh. 2:18; 6:15, 16) Sikuti Nehemiya ankangoyang’anira ntchitoyi koma ankagwira nawo. (Neh. 5:16) Masiku anonso, akulu ambiri amatsanzira Nehemiya pogwira nawo ntchito zomanga kapena kuyeretsa Nyumba za Ufumu. Iwo amalimbitsanso manja a anthu ofooka poyenda nawo mu utumiki komanso kuchita maulendo aubusa.​—Yes. 35:3, 4. w16.09 1:15, 16

Lachitatu, November 14

Chikondi . . . sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha.​—1 Akor. 13:4, 5.

Anthu a Mulungufe timayenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: ‘Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa ndi chilakolako cha kugonana.’ (Akol. 3:2, 5) Sitikufuna kuti Akhristu anzathu azivutika kutsatira malangizowa chifukwa cha zimene timavala. Pali abale ndi alongo amene anasiya khalidwe lachiwerewere koma nthawi zina amalimbanabe ndi maganizo olakwika. (1 Akor. 6:9, 10) Choncho tiyenera kusamala kuti mavalidwe athu asapangitse kuti anthuwa azivutika ndi maganizo olakwikawo. Zovala zimene timavala zizikhala zoti zingathandize kuti mpingo ukhalebe woyera. N’zoona kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha zovala zimene amakonda. Komabe ndi udindo wathu kuvala zovala zimene zingathandize ena kuti aziganiza zoyenera, kulankhula zoyenera komanso kukhala ndi makhalidwe oyera.​—1 Pet. 1:15, 16. w16.09 3:9, 10

Lachinayi, November 15

Anyamata ndi anamwali, . . . atamande dzina la Yehova.—Sal. 148:12, 13.

Banja lina la ku France linati: “Timakhulupirira Yehova, koma zimenezi sizikutanthauza kuti ana athunso azimukhulupirira. Chikhulupiriro si chinthu chomwe munthu amangotengera kwa makolo ake. Ana amayamba kukhala ndi chikhulupiriro pang’onopang’ono.” M’bale wina wa ku Australia analemba kuti: “Kuthandiza ana kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba ndi ntchito yovuta kwambiri. Nthawi zina mungaganize kuti mwayankha bwino funso limene mwana wakufunsani. Koma pakapita nthawi, mumangodabwa kuti akufunsanso funso lomwe lija. Zimenezi zikusonyeza kuti mayankho amene angamufike pamtima lero, pakapita nthawi angakhale osamukhutiritsa. Choncho nkhani zina muyenera kukambirana nawo mobwerezabwereza.” Ngati ndinu kholo, kodi nthawi zina mumaona kuti simungakwanitse udindo wophunzitsa ana anu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba? N’zoona kuti sitingakwanitse ndi nzeru zathu zokha. (Yer. 10:23) Koma tingakwanitse ngati tingadalire Yehova kuti atithandize. w16.09 5:1, 2

Lachisanu, November 16

Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo.​—Miy. 3:27.

Alendo amavutika kusintha zinthu zina kuti azolowere chikhalidwe chatsopano. Koma Rute anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Choyamba, iye anasonyeza kuti ankalemekeza chikhalidwe cha anthu akumene anasamukira popempha kuti akunkhe nawo. (Rute 2:7) Sanaganize kuti anthu ayenera kumulola kukunkha chifukwa choti ndi ufulu wake. Chachiwiri, iye anayamikira chifundo chimene anasonyezedwa. (Rute 2:13) Anthu achilendo akamachita zimenezi amalemekezedwa kwambiri ndi Akhristu anzawo komanso anthu ena. Yehova ndi wokoma mtima kwambiri ndipo walola anthu a mitundu yosiyanasiyana kuti amve uthenga wabwino. Ena mwa anthuwa akanakhalabe m’dziko lawo sakanaphunzira Baibulo kapena kupezeka pamisonkhano yathu. Choncho akafika pamisonkhano tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti azimasuka. w16.10 1:17-19

Loweruka, November 17

Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo.—Aheb. 12:2.

Atumiki ambiri a Mulungu masiku ano akutsanzira Yesu. Iwo amaganizira kwambiri malonjezo a Yehova ndipo amakhalabe okhulupirika akakumana ndi mavuto. Chitsanzo ndi M’bale Rudolf Graichen wa ku Germany amene anabadwa mu 1925. M’baleyu ankakumbukira zithunzi za nkhani za m’Baibulo zimene zinaikidwa m’makoma a nyumba yawo. Iye anati: “Chithunzi china chinkasonyeza mmbulu uli ndi mwana wa nkhosa, mwana wa mbuzi ali ndi kambuku komanso mwana wa ng’ombe ali ndi mkango. Zonse zinkakhala mwamtendere ndipo zinkatsogoleredwa ndi mwana wamng’ono. . . . Sindiiwala zithunzi ngati zimenezi.” (Yes. 11:6-9) Kuganizira mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso kunathandiza m’baleyu kukhalabe wokhulupirika pamene ankazunzidwa ndi chipani cha Nazi komanso cha chikomyunizimu. Koma M’bale Rudolf anakumananso ndi mavuto ena. Mayi ake anamwalira kundende ndi matenda enaake. Komanso bambo ake anafooka n’kusaina chikalata chonena kuti asiya kukhala wa Mboni za Yehova. w16.10 3:12-14

Lamlungu, November 18

Pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.​—1 Ates. 2:13.

Atumiki a Yehova amaona kuti Baibulo ndi buku lapadera kwambiri. Popeza tonsefe ndife ochimwa, nthawi zina timapatsidwa malangizo ochokera m’Malemba. Kodi inuyo mumatani mukapatsidwa malangizo? Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Eodiya ndi Suntuke. Alongo awiriwa anali mumpingo wachikhristu nthawi ya atumwi ndipo anali odzozedwa. Koma zikuoneka kuti anakhumudwitsana kwambiri. Nkhani ya alongowa ikanatha kusokoneza mtendere mumpingo. Baibulo silinena mmene inathera koma n’kutheka kuti anatsatira malangizo amene mtumwi Paulo anawapatsa. (Afil. 4:2, 3) Mavuto oterewa akhoza kuchitikanso mumpingo masiku ano. Koma kutsatira malangizo a m’Baibulo kungatithandize kuti tiwathetse kapena kuwapewa. Zonsezi zingatheke ngati timaona kuti Baibulo ndi buku lapadera ndipo timatsatira malangizo ake.​—Sal. 27:11. w16.11 3:1-3

Lolemba, November 19

Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.​—Miy. 24:10.

Munthu aliyense amafunika kulimbikitsidwa. Mwana akamakula ndi pamenenso amafunika kulimbikitsidwa. Mphunzitsi wina dzina lake Timothy Evans anati: “Ana . . . amafunika kulimbikitsidwa ngati mmene zomera zimafunira madzi kuti zikule bwino. Mwana akalimbikitsidwa amadziona kuti ndi wofunika komanso amadziwa kuti wachita zabwino.” Koma tikukhala m’nthawi yovuta. Anthu ambiri ndi odzikonda, opanda chikondi komanso sakonda kulimbikitsa ena. (2 Tim. 3:1-5) Satana amafuna kutikhumudwitsa n’cholinga choti tifooke pa zinthu zauzimu komanso pa zinthu zina. Satana anachititsa kuti Yobu akumane ndi mavuto ambirimbiri n’cholinga choti afooke, koma Yobu sanafooke. (Yobu 2:3; 22:3; 27:5) Tingalimbane ndi zochita za Mdyerekezi tikamayesetsa kulimbikitsa anthu a m’banja lathu komanso amumpingo wathu. Tikamachita zimenezi, tonse tingamaone kuti panyumba pathu komanso ku Nyumba ya Ufumu ndi malo osangalatsa komanso otetezeka. w16.11 1:4, 6

Lachiwiri, November 20

[Mulungu] anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.​—1 Pet. 2:9.

Anthu ena olimba mtima anachita zinthu zothandiza chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1500. Anthuwa anayamba kumasulira Mawu a Mulungu m’zilankhulo zina. Ndipo Baibulo litayamba kupezeka m’zilankhulo zina, anthu anayambadi kuliwerenga ndipo ankafunsa mafunso monga akuti: Ndi pati m’Baibulo pamene pamapezeka mawu akuti puligatoliyo? Kodi ndi pati pamene pamanena zoti munthu ayenera kulipira kuti wansembe achititse mwambo wa maliro? Nanga zokhudza apapa ndi makadinala zimapezeka pati m’Baibulo? Koma atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri poona kuti anthu anayamba kukayikira zimene tchalitchi chinkaphunzitsa. Choncho anthu amene ankatsutsa ziphunzitso za tchalitchi ankaphedwa. Zonsezi zinkachitika pofuna kulepheretsa anthu kuti asamawerenge Baibulo komanso asamafunse mafunso. Komabe panali anthu ena olimba mtima amene anakana kuti azitsogoleredwa ndi Babulo Wamkulu. Anali atapeza choonadi m’Mawu a Mulungu ndipo ankafuna kudziwa zambiri. w16.11 4:13

Lachitatu, November 21

Mboni yokhulupirika ndi imene sinama.—Miy. 14:5.

Tonsefe timadziwa kuti Akhristu ayenera kuchita zinthu moona mtima. (Aef. 4:25) Baibulo limati Satana ndi “tate wake wa bodza.” Tikudziwanso kuti Hananiya ndi mkazi wake anafa chifukwa ananena zinthu zabodza. Choncho tiyenera kupewa bodza kuti tisafanane nawo. (Yoh. 8:44; Mac. 5:1-11) Koma kodi chofunika n’kupewa kunena zinthu zabodza basi? Ngati timayamikira kukoma mtima kwa Mulungu, tidzayesetsa kukhala oona mtima m’njira zinanso. Munthu akhoza kuchita chinyengo popanda kunena bodza. Mwachitsanzo, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.” Ndiyeno pofotokoza mmene Aisiraeliwo angakhalire oyera, anawauza kuti: “Musabe, musanamizane ndipo aliyense asachitire mnzake chinyengo.” (Lev. 19:2, 11) Chomvetsa chisoni kwambiri n’chakuti anthu ena sanena chilungamo ngakhale kuti sanena bodza lenileni. w16.12 1:17, 18

Lachinayi, November 22

Mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.​—Afil. 4:7.

M’Baibulo timapezamo mawu olimbikitsa a Yesu. Zimene ankaphunzitsa komanso kulankhula zinkathandiza kwambiri anthu amene ankamumvetsera. Anthu ambiri ankapita kwa iye chifukwa ankawalimbikitsa komanso kuwatonthoza. (Mat. 11:28-30) Yesu anasonyeza kuti ankaganiziranso anthu ena. (Maliko 6:30-32) Mawu ake a pa Mateyu 11:28-30 akugwiranso ntchito kwa ifeyo. Ngakhale kuti Yesu salinso padzikoli, angatitsitsimule ngati mmene anachitira ndi atumwi ake. Tikutero chifukwa choti iye ndi Mfumu kumwamba ndipo akupitirizabe kutisonyeza chifundo. Angatithandize “pa nthawi imene tikufunika thandizo” chifukwa cha nkhawa. Choncho tingati Yesu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima, tikhale ndi chiyembekezo komanso tizidziwa zochita tikakhala ndi nkhawa.​—Aheb. 2:17, 18; 4:16. w16.12 3:4, 6

Lachisanu, November 23

Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse.—Gen. 6:13.

Nowa ankakhala m’dziko limene “linadzaza ndi chiwawa” komanso chiwerewere. (Gen. 6:4, 9-12) Ngakhale kuti Nowa ankauza anthu uthenga wochenjeza, sakanatha kukakamiza anthu oipawo kuti amvetsere uthenga wakewo. Iye sakanathanso kupangitsa kuti Chigumula chibwere mwamsanga. Koma iye ankakhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake ndipo adzabweretsa Chigumula pa nthawi yake. (Gen. 6:17) Ifenso tikukhala m’dziko loipa ndipo tikudziwa kuti posachedwapa Yehova aliwononga. (1 Yoh. 2:17) Sitingakakamize anthu kuti azimvetsera ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Palibenso zimene tingachite kuti “chisautso chachikulu” chibwere mwamsanga. (Mat. 24:14, 21) Koma mofanana ndi Nowa, tiyenera kukhulupirira kuti posachedwapa Mulungu awononga dziko loipali. (Sal. 37:10, 11) Tikudziwa kuti nthawi yowononga dzikoli ikadzafika, Yehova sadzalola kuti ipitirire ngakhale ndi tsiku limodzi lokha.​—Hab. 2:3. w17.01 1:5-7

Loweruka, November 24

Ine Yehova ndine . . . amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.​—Yes. 48:17.

Masiku ano anthu ambiri akugwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha, mwina pochitira ena zoipa. Baibulo linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza’ ano anthu ambiri adzakhala “osayamika.” (2 Tim. 3:1, 2) Koma ifeyo tiziyamikira ufuluwu ndipo tizipewa kuugwiritsa ntchito molakwika. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Tonsefe tili ndi ufulu wosankha pa nkhani ya anthu ocheza nawo, zovala, kudzikongoletsa komanso zosangalatsa. Koma ngati titasankha kumangotsatira zofuna zathu kapena ngati timatengeka kwambiri ndi dzikoli, ufulu wathuwu ungakhale ngati “chophimbira zoipa.” (1 Pet. 2:16) Si bwino kugwiritsa ntchito ufulu wathu “polimbikitsira zilakolako za thupi.” M’malomwake tiyeni tiziyesetsa kusankha zochita zimene zingatithandize kutsatira malangizo akuti: “Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”​—Agal. 5:13; 1 Akor. 10:31. w17.01 2:12-14

Lamlungu, November 25

Nditangomva mawu amenewa, . . . ndinasala kudya ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wakumwamba.​—Neh. 1:4.

Chitsanzo cha Nehemiya chikusonyeza kuti kudzichepetsa kungatithandize utumiki wathu ukasintha kapena tikapatsidwa udindo wina. Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti wayamba kudzidalira? Mwachitsanzo, mkulu angayambe kugwira ntchito zina zampingo asanapemphe kaye Yehova kuti amuthandize. Komanso m’bale kapena mlongo angasankhe kuchita zinazake kenako n’kupempha Yehova kuti adalitse zimene wasankhazo. Kodi kumeneku tingati n’kudzichepetsa? Munthu wodzichepetsa sadalira nzeru zake ngakhale zitakhala kuti zimene akufuna kuchitazo si koyamba kuzichita. Amakumbukira kuti nzeru zake n’zochepa kwambiri poyerekeza ndi za Yehova ndipo amadziwa malo ake m’gulu la Yehova. (Miy. 3:5, 6) Anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda ndipo amafuna kukhala oposa ena. Koma atumiki a Yehovafe sitichita zimenezi. Timachita zinthu mogwirizana ndipo sitiganiza kuti udindo m’banja kapena mumpingo umapangitsa kuti munthu akhale wapamwamba kuposa ena.​—1 Tim. 3:15. w17.01 4:7, 8

Lolemba, November 26

Dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.​—Sal. 115:16.

Cholinga cha Yehova chinali chakuti anthu azikhala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Iye anapatsa Adamu ndi Hava mphatso zosiyanasiyana zowathandiza kuti azisangalala. (Yak. 1:17) Yehova anawapatsa ufulu wosankha zochita, nzeru komanso mtima wotha kukonda anzawo. Mulungu anapereka malangizo kwa Adamu omuthandiza kuti azimumvera. Anamuphunzitsanso mmene angapezere zofunika pa moyo wake komanso mmene angasamalirire dziko ndi zinyama. (Gen. 2:15-17, 19, 20) Yehova analenganso Adamu ndi Hava m’njira yoti azitha kuona, kumva, kununkhiza, kuzindikira zimene zawakhudza komanso kumva kukoma kwa chakudya. Izi zinachititsa kuti azisangalala ndi zinthu m’Paradaiso. Anthu oyambirirawa anali ndi ntchito zosangalatsa komanso zinthu zatsopano zoti aphunzire. Yehova anawalenganso m’njira yoti abereke ana angwiro. Iye anawapatsa dziko lapansili ndi zinthu zonse zimene zilimo kuti akhalemo mpaka kalekale. w17.02 1:6, 7

Lachiwiri, November 27

Ayenera kukopera buku lakelake la chilamulo ichi . . . ndi kusunga mawu onse a chilamulo ichi.—Deut. 17:18, 19.

Kodi Mawu a Mulungu anathandiza bwanji anthu amene ankatsogolera Aisiraeli? Tiyeni tione chitsanzo cha Mfumu Yosiya. Buku la Chilamulo litapezeka, mlembi wake anayamba kumuwerengera. Ndiye kodi iye anatani? “Mfumuyo itangomva mawu a m’buku la chilamulolo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.” Yosiya anayambanso chintchito chothetsa kulambira mafano komanso anakonza zoti achite chikondwerero chachikulu cha Pasika. (2 Maf. 22:11; 23:1-23) Popeza kuti Yosiya ndi atsogoleri ena okhulupirika ankatsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu, anali ofunitsitsa kusintha malangizo amene ankapatsa anthu a Mulungu. Kusintha kumeneku kunathandiza kuti Aisiraeli azichita zinthu zimene Mulungu amafuna. Komabe si mafumu onse a anthu a Mulungu amene ankatsatira malangizo a Mulunguyo. Ndipo mafumu amene sankamvera Yehova ankakana kutsogoleredwa ndi mzimu woyera, angelo komanso Mawu a Mulungu. Zikatero, Yehova ankawalanga kapena kuwachotsa pa udindo. (1 Sam. 13:13, 14) Pa nthawi yake, Yehova anasankha mtsogoleri wabwino kuposa wina aliyense. w17.02 3:11, 12, 14

Lachitatu, November 28

Munamuchepetsa [munthu] pang’ono poyerekeza ndi ena onga Mulungu, Kenako munamuveka ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu.​—Sal. 8:5.

Anthufe tinalengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.” (Gen. 1:27) N’chifukwa chake anthu ambiri amasonyeza makhalidwe a Mulungu. Mwachitsanzo, anthu amatha kusonyezana chikondi, kukoma mtima komanso chifundo. Popeza anthu analengedwa ndi chikumbumtima, amatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera, zachilungamo ndi zachinyengo ndiponso zabwino ndi zoipa. (Aroma 2:14, 15) Komanso anthu ambiri amasangalala ndi zinthu zaukhondo ndiponso zokongola. Anthufe timafunanso kukhala mwamtendere ndi ena. Choncho, kaya modziwa kapena mosadziwa, anthu amasonyeza ulemerero wa Mulungu mwa njira inayake. Chifukwa cha zimenezi anthu ayenera kupatsidwa ulemu ngakhale kuti sungafanane ndi umene timapatsa Yehova kapena Yesu. Koma pa nkhaniyi tiyenera kudziwa zoyenera ndi zosayenera kuchita. w17.03 1:5, 6

Lachinayi, November 29

Mulungu woona anasintha maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.​—Yona 3:10.

Mulungu sali ngati anthu amene amasankha zochita mopupuluma chifukwa choti akwiya kapena akhumudwa. Iye ataona kuti anthu a ku Nineve alapa, anasintha zimene ankafuna kuchita. Apatu anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa, wachifundo komanso amamvetsa zinthu. Nafenso nthawi zina tingafunike kuganiziranso zimene tinasankha. Ngati zinthu zina zasintha, ifenso tikhoza kusintha. Nayenso Yehova amasintha maganizo zinthu zikasintha. (1 Maf. 21:20, 21, 27-29; 2 Maf. 20:1-5) Mwachitsanzo, tikadziwa mfundo ina yatsopano tikhoza kusintha zimene tinasankha. Izi n’zimene zinachitikira Mfumu Davide. Poyamba anauzidwa zinthu zabodza zokhudza mdzukulu wa Sauli dzina lake Mefiboseti. Koma atamva zoona zake anasintha zimene anasankha poyamba.​—2 Sam. 16:3, 4; 19:24-29. w17.03 2:14, 15

Lachisanu, November 30

Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.​—Afil. 4:5.

Tikakumana ndi vuto tiyenera kufufuza mfundo zonse za m’Baibulo zimene zikukhudzana ndi vutolo n’kuona kuti tingazitsatire bwanji. Tiyerekeze kuti pali mlongo wina amene mwamuna wake si Mboni. Mlongoyu akudziwa kuti ayenera kumalalikira uthenga wabwino. (Mac. 4:20) Ndiyeno wakonza zoti tsiku lina adzalowe mu utumiki. Koma mwamuna wake akufuna kuti pa tsikulo adzapitire limodzi kwinakwake. Mwamunayo akuona kuti n’kale pamene anakhalapo ndi nthawi yochita zinthu limodzi. Mkaziyo angaganizire lamulo la Yesu loti tiziphunzitsa anthu komanso mfundo yakuti tiyenera kumvera Mulungu. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29) Koma angachitenso bwino kuganizira mfundo yakuti akazi ayenera kugonjera amuna awo ndiponso azikhala ololera. (Aef. 5:22-24) Kodi mwamuna wakeyo amamuletsa kupita kolalikira kapena akungofuna kuti pa tsikuli asachoke kuti achitire limodzi zinthu zina? Chitsanzochi chikusonyeza kuti tiyenera kukhala osamala pochita zinthu kuti tizikhala ndi chikumbumtima chabwino potumikira Mulungu. w17.03 4:17

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena