Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es18 tsamba 118-128
  • December

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2018
  • Timitu
  • Loweruka, December 1
  • Lamlungu, December 2
  • Lolemba, December 3
  • Lachiwiri, December 4
  • Lachitatu, December 5
  • Lachinayi, December 6
  • Lachisanu, December 7
  • Loweruka, December 8
  • Lamlungu, December 9
  • Lolemba, December 10
  • Lachiwiri, December 11
  • Lachitatu, December 12
  • Lachinayi, December 13
  • Lachisanu, December 14
  • Loweruka, December 15
  • Lamlungu, December 16
  • Lolemba, December 17
  • Lachiwiri, December 18
  • Lachitatu, December 19
  • Lachinayi, December 20
  • Lachisanu, December 21
  • Loweruka, December 22
  • Lamlungu, December 23
  • Lolemba, December 24
  • Lachiwiri, December 25
  • Lachitatu, December 26
  • Lachinayi, December 27
  • Lachisanu, December 28
  • Loweruka, December 29
  • Lamlungu, December 30
  • Lolemba, December 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2018
es18 tsamba 118-128

December

Loweruka, December 1

Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye, podziwa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumana ndi masautso ngati omwewo.—1 Pet. 5:9.

Petulo analembera Akhristu mawu amenewa pofuna kuwalimbikitsa kuti apirire mayesero. Zitsanzo za “amene anapirira” zimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti nafenso tipirire. Zimatitsimikiziranso kuti nafenso tingathe kupirira ndipo tidzadalitsidwa tikakhalabe okhulupirika. (Yak. 5:11) Kodi mukuzunzidwa chifukwa chotumikira Mulungu? Kodi ndinu mkulu kapena woyang’anira dera ndipo mukuona kuti muli ndi ntchito yambiri? Chitsanzo cha Paulo chingakuthandizeni. Iye anakumana ndi mavuto aakulu ochokera kwa adani ake komanso ankadera nkhawa kwambiri za abale ndi alongo a m’mipingo yonse. (2 Akor. 11:23-29) Koma Paulo sanafooke ndipo chitsanzo chake chinalimbikitsanso ena. (2 Akor. 1:6) Ngati inunso mukukumana ndi mavuto, dziwani kuti mukakhalabe okhulupirika mukhoza kulimbikitsa Akhristu anzanu. w16.04 2:11, 14

Lamlungu, December 2

Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.​—Mat. 28:19, 20.

Ngakhale kuti anthu ena amatsutsa uthenga wathu, ambiri amavomereza kuti a Mboni za Yehova amadziwika ndi ntchito yolalikira. Mwina mwakumanapo ndi anthu ena amene amati ngakhale kuti sagwirizana ndi zimene timalalikira, amaona kuti timachita bwino kulalikira. Yesu ananeneratu kuti uthenga wabwino wa Ufumu uyenera kulalikidwa padziko lonse. (Mat. 24:14) Anthu a zipembedzo zambiri amati amalalikira uthenga wabwino. Koma nthawi zambiri amangolalikira m’tchalitchi, pawailesi, pa TV, pa Intaneti kapenanso kwa munthu mmodzi. Ena amati amalalikira pothandiza ovutika, pomanga zipatala kapena masukulu. Koma kodi izi n’zimene Yesu ankatanthauza pamene anati otsatira ake azilalikira? w16.05 2:1, 2

Lolemba, December 3

Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!​—Mac. 25:11.

Kuyambira mu 1914, maboma a anthu akhala akuchita zinthu zotsutsana ndi Ufumu wa Mulungu. Koma posachedwapa Ufumuwu udzawononga maboma onse. (Sal. 2:2, 7-9) Yehova walola kuti maboma akhalepo n’cholinga choti azikhazikitsa bata. Izi zimathandiza kuti tizilalikira bwinobwino. (Aroma 13:3, 4) Paja Yehova amatiuzanso kuti tizipempherera olamulirawa makamaka ngati zimene angasankhe zingakhudze kulambira kwathu. (1 Tim. 2:1, 2) Mofanana ndi Paulo, timathanso kupempha thandizo la boma ngati ena sanatichitire zachilungamo. Baibulo limanena kuti dziko lonse lili m’manja mwa Satana. Koma silinena kuti iye amalamulira mwachindunji munthu aliyense amene ali m’boma. (Luka 4:5, 6) Choncho si bwino kunena kuti wolamulira wakutiwakuti akutsogoleredwa ndi Mdyerekezi. Tizipewanso kunenera zoipa “maboma ndiponso olamulira.”​—Tito 3:1, 2. w16.04 4:5, 6

Lachiwiri, December 4

Pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.​—Aef. 5:17.

Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingadziwe bwanji zimene Yehova angasangalale nazo ngati palibe lamulo la m’Baibulo pa nkhaniyo?’ Ndiye kodi tingazindikire bwanji chifuniro cha Yehovacho? Tiyenera kupemphera kwa iye komanso kulola kuti mzimu wake uzititsogolera. Yesu ankazindikira zimene Atate wake ankafuna kuti iye azichita. Mwachitsanzo, kawiri konse iye anapemphera kwa Yehova ndipo anachulukitsa chakudya n’kukwanira anthu ambirimbiri. (Mat. 14:17-20; 15:34-37) Koma pamene Mdyerekezi anamuyesa m’chipululu anakana kusandutsa miyala kuti ikhale mikate ngakhale kuti anali ndi njala. (Mat.4:2-4) Chifukwa chakuti amadziwa maganizo a Atate wake, sanalole zimenezi. Yesu anazindikira kuti Yehova sangasangalale ngati iyeyo atagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti apeze zimene akufuna. Choncho pokana kusandutsa miyala kukhala mikate, anasonyeza kuti ankadalira Yehova kuti azimutsogolera komanso kum’patsa zofunika pa moyo. w16.05 3:7, 8

Lachitatu, December 5

Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.—2 Tim. 3:16.

N’zoona kuti nkhani zina za m’Baibulo analembera anthu enaake kapena gulu linalake la anthu. Choncho tisanayambe kuwerenga Baibulo, tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kumvetsa mfundo zomwe iyeyo akufuna kuti tiphunzire. (Ezara 7:10; Yak. 1:5) Mukamawerenga nkhani inayake m’Baibulo, muzidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova? Kodi mfundo zimenezi ndingazigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanga? Nanga ndingazigwiritse ntchito bwanji pothandiza ena? Tikamaganizira mafunsowa, Baibulo lingatithandize kwambiri. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Malemba amanena kuti akulu azichita. (1 Tim. 3:2-7) Popeza kuti ambirife si ife akulu, mwina tingamaganize kuti mfundo za m’lembali sizikutikhudza kwenikweni koma zikhoza kutithandiza. w16.05 5:7, 8

Lachinayi, December 6

Taonani! Mofanana ndi dongo limene lili m’manja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine.​—Yer. 18:6.

Ayuda atatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, anapeza kuti anthu a mumzindawo ankakonda kulambira mafano komanso ankachita zamizimu. Komabe Ayuda okhulupirika, monga Danieli ndi anzake atatu sanalole kuumbidwa ndi anthu a ku Babulo. (Dan. 1:6, 8, 12; 3:16-18) Danieli ndi anzakewo ankafunitsitsa kuti aziumbidwa ndi Yehova yekha basi. Zimenezi zinathekadi chifukwa ngakhale kuti Danieli anakhala ku Babulo pafupifupi kwa moyo wake wonse, mngelo wa Mulungu ananena kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri.” (Dan. 10:11, 19) Kale, woumba ankatenga dongo n’kulikanikiza pachinthu chinachake kuti aumbe chimene akufuna. Masiku ano atumiki a Yehova amadziwa kuti Yehova ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ndipo ali ndi mphamvu zoti angaumbe mitundu ya anthu. (Yer. 18:6) Mulungu akhozanso kuumba munthu aliyense payekha. Komabe iye amalemekeza ufulu wosankha zochita umene anthufe tili nawo ndipo amafuna kuti tizimumvera mwakufuna kwathu. w16.06 2:1, 2

Lachisanu, December 7

Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama.​—Aheb. 13:5.

Satana amagwiritsa ntchito anthu otsatsa malonda pofuna kutikopa. Amafuna tiziganiza kuti tingakhale osangalala tikakhala ndi zinthu zambiri. Iye amagwiritsa ntchito “chilakolako cha maso.” (1 Yoh. 2:15-17; Gen. 3:6; Miy. 27:20) Dzikoli lili ndi zinthu zosiyanasiyana, zina zabwino koma zina zachabechabe, ndipo zina zimaoneka zokopa kwambiri. Kodi inuyo munagulapo chinthu chosafunika kwenikweni chifukwa choti anachitsatsa kapena munangochiona musitolo? Kodi munazindikira kuti mukanatha kukhala bwinobwino popanda chinthucho? Zinthu zosafunika kwenikweni ngati zimenezo zimangochititsa kuti tizikhala ndi nkhawa. Zikhoza kutilepheretsa kuchita zinthu zofunika monga kuphunzira Baibulo, kukonzekera komanso kupezeka pamisonkhano ndiponso kulalikira. Tisaiwale chenjezo la mtumwi Yohane lakuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” w16.07 1:3, 4

Loweruka, December 8

Ilipodi “milungu” yambiri . . . kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi.​—1 Akor. 8:5, 6.

Mumpingo wachikhristu woyambirira munali Ayuda, Agiriki, Aroma komanso anthu a mitundu ina. Poyamba anthuwa anali osiyana zikhulupiriro, miyambo komanso zokonda. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ena azivutika kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Ankavutikanso kuti asiye zinthu zina zimene ankachita poyamba. Choncho mtumwi Paulo anawakumbutsa kuti Akhristu onse ali ndi Mulungu mmodzi, Yehova. Nanga kodi zinthu zili bwanji mumpingo wachikhristu masiku ano? Mneneri Yesaya ananeneratu kuti “m’masiku otsiriza,” anthu ochokera m’mitundu yonse adzayamba kulambira Yehova. Iwo adzanena kuti: ‘[Yehova] adzatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.’ (Yes. 2:2, 3) Ndi zosangalatsa kuona kuti ulosiwu ukukwaniritsidwa masiku ano. M’mipingo mumapezeka abale ndi alongo a mitundu, zilankhulo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Koma tonse timalambira Yehova mogwirizana. w16.06 3:15, 16

Lamlungu, December 9

Anatikweza pamodzi, ndi kutikhazika pamodzi m’malo akumwamba mogwirizana ndi Khristu Yesu.—Aef. 2:6.

Pali madalitso ambiri amene Yehova wasungira odzozedwa kumwamba akadzakhala m’mipando yachifumu n’kumalamulira limodzi ndi Khristu. (Luka 22:28-30; Afil. 3:20, 21; 1 Yoh. 3:2) Yehova ‘adzawasonyeza chuma chopambana cha kukoma mtima kwake kwakukulu.’ Odzozedwawa adzakhala “Yerusalemu Watsopano” kapena kuti mkazi wophiphiritsa wa Khristu. (Chiv. 3:12; 17:14; 21:2, 9, 10) Iwo limodzi ndi Yesu adzagwira ntchito ‘yochiritsa mitundu ya anthu,’ kutanthauza kuti adzawathandiza kuti amasuke ku uchimo ndi imfa n’kukhala angwiro. (Chiv. 22:1, 2, 17) Njira ina imene Yehova adzasonyezere kukoma mtima kwakukulu ndi kuukitsa anthu amene ali “m’Manda.” (Yobu 14:13-15; Yoh. 5:28, 29) Anthu okhulupirika amene anamwalira Khristu asanatifere adzaukitsidwa n’kuyambanso kutumikira Yehova. Nawonso a “nkhosa zina” amene amamwalira ali okhulupirika m’masiku otsiriza ano, adzaukitsidwa.​—Yoh. 10:16. w16.07 4:13-15

Lolemba, December 10

Koma zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula!—Maliko 14:41.

Kuti ‘tikhale maso’ pamafunika zambiri osati kungokhala ndi maganizo abwino. Masiku angapo asanapite m’munda wa Getesemane, Yesu anauza atumwiwo kuti azipemphera kwa Yehova mopembedzera. (Luka 21:36) Choncho kuti tikhale maso, nafenso tiyenera kumapemphera nthawi zonse. (1 Pet. 4:7) Paja Yesu ananena kuti mapeto adzafika ‘pa ola limene sitikuliganizira.’ (Mat. 24:44) Choncho ino si nthawi yoti tizifunafuna moyo umene dzikoli limaona kuti ungachititse munthu kukhala wosangalala. Zimenezo zingapangitse kuti tiyambe kusinza mwauzimu. M’Baibulo timapeza malangizo ochokera kwa Yehova ndi Yesu amene angatithandize kuti tikhalebe maso. Choncho tiyeni tiziganizira maulosi a m’Baibulo amene akukwaniritsidwa panopa komanso kukwaniritsidwa kwake. Tizionetsetsanso kuti tili pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso tikuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. Tikatero mapeto adzatipeza tili okonzeka ndipo tidzapulumuka.​—Chiv. 22:20. w16.07 2:15-17

Lachiwiri, December 11

Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.—Akol. 3:13.

Banja limalimba ngati anthu okwatirana amakumbukira kuti aliyense ndi wochimwa komanso ‘amalolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.’ Aliyense m’banja angalakwitse zinazake. Koma zoterezi zikachitika, ndi bwino kuphunzirapo kanthu, kukhululukirana komanso kusonyezana chikondi. Paja chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akol. 3:14) Komanso ‘chikondi n’choleza mtima, chokoma mtima ndipo sichisunga zifukwa.’ (1 Akor. 13:4, 5) Pakakhala kusagwirizana, anthu okwatirana ayenera kuthetsa vutolo lisanafike tsiku lotsatira. (Aef. 4:26, 27) Pamafunika kudzichepetsa komanso kulimba mtima kuti munthu anene mochokera pansi pa mtima kuti, “Pepani mundikhululukire.” Koma izi zimathandiza kuti anthu okwatirana azithetsa mavuto komanso azigwirizana. w16.08 2:6

Lachitatu, December 12

Ndidzakupatsani malangizo abwino.​—Miy. 4:2.

Ntchito yaikulu ya Yesu inali yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Koma iye ankapezanso nthawi yothandiza ena kuti akhale aphunzitsi komanso abusa. (Mat. 10:5-7) Filipo ankalalikira mwakhama koma ankapezanso nthawi yophunzitsa ana ake aakazi kuti azilalikira mogwira mtima. (Mac. 21:8, 9) Nanga bwanji masiku ano? Kodi kuphunzitsa ena n’kofunika bwanji? Masiku ano pali anthu ambiri amene akufuna kuphunzira Baibulo. Komanso tiyenera kuthandiza ofalitsa osabatizidwa kuti azikonda kuphunzira Baibulo paokha. Tiyenera kuwathandizanso kuti azilalikira ndi kuphunzitsa mwaluso. Kuwonjezera pamenepo, abale amafunika kuwathandiza kuti ayenerere kukhala akulu kapena atumiki othandiza. Choncho tikamapereka “malangizo abwino,” tidzathandiza atsopano kuti achite zambiri m’gulu la Yehova. w16.08 4:1, 2

Lachinayi, December 13

Anthu inu limbitsani manja ofooka ndiponso mawondo agwedegwede.​—Yes. 35:3.

Tikamatumikira limodzi ndi abale ndi alongo athu, timakhala ogwirizana. Zimathandizanso kuti tizikondana kwambiri komanso kuti tiziyembekezera madalitso amene tidzapeze mu Ufumu wa Mulungu. Tikamayesetsa kulimbitsa manja awo, timawathandiza kuti asafooke komanso kuti azikhulupirira zoti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. (Yes. 35:4) Izi zimathandiza kuti nafenso tizikonda zinthu zauzimu komanso tizikhulupirira kwambiri kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake. Choncho tingati ifenso manja athu amalimba. Kuganizira mmene Yehova anathandizira atumiki ake okhulupirika atakumana ndi mavuto kungatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tizimudalira kwambiri. Choncho mukakumana ndi mavuto, muzipemphera kwa Yehova ndipo musamalole kuti manja anu ‘alefuke.’ (Zef. 3:16) Musamakayikire kuti iye adzakuthandizani ndi dzanja lake lamphamvu kuti mupirire n’kudzalandira madalitso mu Ufumu wake.​—Sal. 73:23, 24. w16.09 1:16-18

Lachisanu, December 14

[Pali] nthawi yochitira chinthu chilichonse ndiponso yokhudza ntchito iliyonse.—Mlal. 3:17.

Akhristu akamasankha zovala amakumbukira mfundo yamulemba la leroyi. N’zoona kuti pa nkhani ya zovalayi timaganiziranso nyengo. Nthawi zinanso anthu amavala mosiyana ndi anzawo chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wawo komanso mmene nyengo yasinthira. Komabe tizikumbukira kuti mfundo za Yehova sizisintha chifukwa cha nyengo. (Mal. 3:6) M’madera otentha, zimakhala zovuta kuti anthu asankhe mwanzeru zovala zimene zingapereke ulemu. Komabe abale ndi alongo amayamikira tikamayesetsa kupewa zovala zothina komanso zoonetsa mkati. (Yobu 31:1) Komanso zovala zimene timavala kunyanja kapena malo ena osambirira ziyenera kukhala zoyenera. (Miy. 11:2, 20) Ngakhale kuti anthu ambiri a m’dzikoli akakhala kunyanja savala bwino, Akhristufe timaona kuti tiyenera kuvala moyenera kuti tikondweretse Mulungu wathu woyera amene timamukonda. w16.09 3:11, 12

Loweruka, December 15

Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?”​—Mat. 16:15.

Yesu ankafunsa otsatira ake kuti adziwe zimene amakhulupirira. Inunso mungachite bwino kufunsa ana anu kuti azifotokoza maganizo awo. Ngati mwana wanu akukayikira mfundo zina, musamafulumire kumukalipira kapena kumutsutsa. Muyenera kukambirana naye moleza mtima. Akafunsa mafunso okhudza nkhani inayake ndiye kuti akufuna kuimvetsa bwino. Musaiwale kuti Yesu ali ndi zaka 12 ankafunsa mafunso anzeru. (Luka 2:46) Yesetsani kuti muwadziwe bwino ana anu. Muyenera kudziwa zimene amaganizira, zimene zimawasangalatsa komanso zomwe zimawadetsa nkhawa. Musaganize kuti ali ndi chikhulupiriro chifukwa choti amapezeka pamisonkhano ndiponso amalalikira. Mukamachita nawo zinthu tsiku ndi tsiku, muzipezanso mpata wokambirana nawo zinthu zauzimu. Muzipemphera nawo komanso muziwapempherera. Muziyesetsanso kudziwa mayesero amene akukumana nawo ndipo muziwathandiza kuthana ndi mayeserowo. w16.09 5:3-5

Lamlungu, December 16

Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.—Mat. 5:3.

Masiku ano, abale ndi alongo ambiri akuthandiza pokwaniritsa ulosi woti uthenga wabwino udzalalikidwa “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Kodi inuyo mukuphunzira chilankhulo china? Kodi ndinu mmishonale kapena mumasonkhana mumpingo wa chilankhulo china? Atumiki a Yehovafe tiyenera kuzindikira kuti chofunika kwambiri n’kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso cha banja lathu. Koma nthawi zina timatanganidwa kwambiri moti sitipeza nthawi yophunzira patokha bwinobwino. Koma anthu amene amasonkhana mumpingo wa chilankhulo china amakhalanso ndi mavuto ena. Iwo amafunika kuphunzira chilankhulo chatsopano komanso kuonetsetsa kuti mfundo zozama za m’Mawu a Mulungu zikuwafika pamtima.—1 Akor. 2:10. w16.10 2:1-3

Lolemba, December 17

Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.​—Mat. 26:52.

A Mboni za Yehova amasangalalabe akaganizira zimene akuyembekezera ngakhale kuti amazunzidwa kwambiri. Mwachitsanzo, pali abale ndi alongo amene ali m’ndende ku Eritrea, ku Singapore ndi ku South Korea. Ambiri mwa anthuwa anamangidwa chifukwa chomvera mawu a Yesu akuti tisamamenye nkhondo. Sikuti atumiki a Yehova onse akukumana ndi mavuto oterewa. Ena amakumana ndi mayesero a mtundu wina. Mwachitsanzo, ena amavutika ndi umphawi, nkhondo kapena ngozi zadzidzidzi. Ena ali ngati atumiki a Mulungu akale monga Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Mose. Iwo alolera kusiya moyo wawofuwofu n’cholinga choti atumikire Mulungu ndipo amapewa mtima wodzikonda komanso wokonda chuma. Kodi amatha bwanji kuchita zonsezi? Iwo amakonda kwambiri Yehova ndipo sakayikira lonjezo lake loti adzathetsa mavuto onse ndiponso loti anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lachilungamo.​—Sal. 37:5, 7, 9, 29. w16.10 3:15, 16

Lachiwiri, December 18

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.​—Sal. 34:18.

Pamene Yeremiya anafooka komanso kuchita mantha, Yehova anamulimbikitsa. (Yer. 1:6-10) Komanso kodi mukuganiza kuti mneneri Danieli anamva bwanji pamene Mulungu anatumiza mngelo kukamulimbikitsa? Mngeloyo anatchula Danieli kuti “munthu wokondedwa kwambiri.” (Dan. 10:8, 11, 18, 19) Nanunso mungathe kulimbikitsa ofalitsa, apainiya komanso abale ndi alongo amene akufooka chifukwa cha uchikulire. Paja Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kumwamba kwa zaka zambirimbiri. Komabe pamene Yesu anali padzikoli, Yehova sanaganize kuti Mwana wakeyu sankafunika kuyamikiridwa komanso kulimbikitsidwa. M’malomwake Yesu atangoyamba kumene utumiki wake komanso chakumapeto kwa utumikiwo, Yehova analankhula kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:17; 17:5) Apa Mulungu anayamikira Mwana wakeyu komanso anamutsimikizira kuti akuchita zabwino. Usiku woti Yesu afa mawa, Yehova anatumizanso mngelo kuti akamulimbikitse chifukwa anali ndi nkhawa kwambiri.​—Luka 22:43. w16.11 1:7, 8

Lachitatu, December 19

Usamafulumire kukwiya mumtima mwako.​—Mlal. 7:9.

Kunena zoona, si zapafupi kuugwira mtima munthu wina akatilakwira. Zimakhala zowawa ngati munthu watichitira zopanda chilungamo chifukwa choti timasiyana naye mtundu kapena chikhalidwe. Ndiyeno nkhaniyi imakhala yaikulu kwambiri ngati watilakwirayo ndi Mkhristu mnzathu. Anthufe tikakhumudwa kapena kukwiya tikhoza kuchita zinthu zimene pambuyo pake tinganong’oneze nazo bondo. N’chifukwa chake Baibulo limatilangiza kuti tiziugwira mtima komanso tisamafulumire kukwiya. (Miy. 16:32) Koma Baibulo limatilimbikitsanso kuti tikhale ndi mtima wokhululuka. Paja Yesu ananena kuti ngati sitikhululukira anzathu, ifenso Yehova sadzatikhululukira. (Mat. 6:14, 15) Kodi inuyo mumaona kuti zimakuvutani kuugwira mtima kapena kukhulululukira anzanu? Anthu amene amalephera kuugwira mtima amakwiyakwiya ndipo akhoza kuyamba kudana ndi anzawo. Anthu oterewa akhoza kuyambitsa mavuto mumpingo.—Lev. 19:17, 18. w16.11 3:4-6

Lachinayi, December 20

Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?—2 Akor. 6:14.

Charles Taze Russell ndi anzake anayamba kuphunzira Baibulo m’zaka za m’ma 1800. Poyamba cholinga cha M’bale Russell chinali kufufuza kuti adziwe chipembedzo chimene chimaphunzitsa choonadi. Choncho anayerekezera zimene matchalitchi ambiri amaphunzitsa ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Anafufuzanso ngakhale m’zipembedzo zomwe si zachikhristu. Koma anapeza kuti palibe chipembedzo chimene chinkaphunzitsa zogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Pa nthawi ina anauza atsogoleri achipembedzo angapo mfundo za m’Baibulo zimene iye ndi anzake aja anapeza. Ankaganiza kuti iwo agwirizana nazo ndipo ayamba kuphunzitsa zimenezi m’matchalitchi awo. Koma atsogoleri achipembedzowo sanasonyeze chidwi. Choncho Ophunzira Baibulowa anazindikira kuti sangathe kulambira Mulungu ndi anthu amene ali m’chipembedzo chonyenga. w16.11 4:14

Lachisanu, December 21

Perekaninso ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a chilungamo kuti muzichita ntchito za chiyero.—Aroma 6:19.

Munthu amene amayamikira kukoma mtima kwa Mulungu amapewa dama, kuledzera komanso machimo ena amene ankachitika ku Korinto. (1 Akor. 6:9-11) Koma si zokhazi. Ayenera kupewanso chilichonse chimene chingakhumudwitse Yehova. Mwachitsanzo, m’malo mongopewa chiwerewere, ayenera kupewanso zosangalatsa zimene zimalimbikitsa chiwerewerecho. M’malo mopewa kuledzera amapewanso kumwa kwambiri moti n’kutsala pang’ono kuledzera. N’zoona kuti kuchita zimenezi si kophweka koma ndi nkhondo yoti tikhoza kupambana. Tiyeni tiziyesetsa kupewa machimo akuluakulu komanso ang’onoang’ono. N’kutheka kuti nthawi zina tizilephera kuchita zimenezi bwinobwino. Koma tiyenera kuyesetsa ngati mmene Paulo ankachitira. Paja iye anauza Akhristu anzake kuti: “Musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo.”​—Aroma 6:12; 7:18-20. w16.12 1:16, 19-21

Loweruka, December 22

Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.—Agal. 5:22, 23.

Yesu ananena kuti Atate wathu wakumwamba adzapereka mzimu woyera kwa anthu amene amamupempha. (Luka 11:10-13) Mzimuwu umatithandiza kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu ali nawo. (Akol. 3:10) Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri amene mzimu woyera umatulutsa, timagwirizana kwambiri ndi anzathu. Zimenezi zimathandiza kuti tipewe zinthu zimene zikanatibweretsera nkhawa. Tiyenera kukhala odzichepetsa kuti tizidalira “dzanja lamphamvu la Mulungu” komanso kuti ‘tizimutulira nkhawa zathu zonse.’ (1 Pet. 5:6, 7) Kudzichepetsa kumatithandiza kuzindikira kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kuchita. (Mika 6:8) Choncho m’malo modalira mphamvu ndi nzeru zathu, timadalira Yehova kuti azitithandiza. Ndiyeno tikaona kuti akutithandiza komanso kutikonda, sitida nkhawa kwambiri. w16.12 3:7, 12

Lamlungu, December 23

Nowa [anali] mlaliki wa chilungamo.​—2 Pet. 2:5.

Nowa anali “mlaliki wa chilungamo” ndipo ankagwira mokhulupirika ntchito yochenjeza anthu imene Mulungu anamupatsa. Izi ziyenera kuti zinamuthandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Kuwonjezera pa ntchito yolalikira, Nowa ankagwiranso ntchito yomanga chingalawa. (Aheb. 11:7) Nafenso timayesetsa kuti tizichita ‘zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Ntchito ina imene tingagwire ndi yomanga nawo Nyumba za Ufumu kapena Malo a Misonkhano. Tingathenso kugwira nawo mongodzipereka ntchito zina pamisonkhano yadera komanso yachigawo. Tikhozanso kukatumikira pa Beteli kapena kumaofesi a omasulira mabuku. Koma ntchito yofunika kwambiri imene timagwira ndi yolalikira ndipo imatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachidule tingati ntchito yolalikira imatithandiza kuti tipitirizebe kuthamanga pa mpikisano wokalandira moyo.​—1 Akor. 9:24. w17.01 1:8, 9

Lolemba, December 24

Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.

Tiyenera kulemekeza ufulu wa anthu ena wosankha zochita. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Popeza aliyense ali ndi mphatsoyi, sizingatheke kuti nthawi zonse tizisankha zinthu zofanana. Akhristu angasankhe zosiyana ngakhale pa nkhani zokhudza kulambira. Kukumbukira kuti Mkhristu aliyense ayenera “kunyamula katundu wake,” kungatithandize kuti tizilemekeza ufulu wa ena wosankha zochita, ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono. (1 Akor. 10:32, 33) Yehova anatipatsa mphatso ya ufulu wosankha zochita ndipo izi zimachititsa kuti tikhale ndi ufulu weniweni. (2 Akor. 3:17) Timayamikira mphatsoyi chifukwa imatithandiza kuti tizitha kusankha zinthu zimene zimasonyeza kuti timakonda Yehova. Tiyeni tipitirize kuyamikira mphatsoyi polemekeza Mulungu komanso polemekeza zimene anthu ena asankha. w17.01 2:15, 17, 18

Lachiwiri, December 25

Sindichita kanthu mongoganiza ndekha. Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.—Yoh. 8:28.

Munthu wodzichepetsa amapewa kudzionetsera kapena kudzitama koma amasonyeza “mzimu wabata ndi wofatsa.” (1 Pet. 3:3, 4; Yer. 9:23, 24) Zimene timachita komanso kulankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, anthu ena amakonda kulankhula zosonyeza kuti akusangalala chifukwa choti ali ndi udindo winawake, akudziwa zinsinsi zina kapena chifukwa choti amagwirizana ndi abale ena audindo. Ena amakonda kulankhula zosonyeza kuti zinthu zina zinayenda bwino chifukwa cha iwowo n’kuiwala kuti ena anathandizaponso. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzichepetsa. Mfundo zambiri zimene ankalankhula zinali zochokera m’Malemba Achiheberi kapena zokhudza Malembawo. Iye ankachita zimenezi n’cholinga choti anthu adziwe kuti zimene ankalankhula zinali zochokera kwa Yehova osati nzeru zake. w17.01 4:12

Lachitatu, December 26

Usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.—Gen. 2:17.

Lamuloli linali lomveka bwino komanso losavuta kulitsatira. Ndipotu Adamu ndi Hava anali ndi chakudya cha mwanaalirenji. Satana anagwiritsa ntchito njoka popusitsa Hava kuti asamvere Atate wake Yehova. (Gen. 3:1-5; Chiv. 12:9) Choyamba Satana anafunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Zinali ngati akuwafunsa kuti: ‘Ndiye kuti mulibe ufulu wochita zimene mukufuna?’ Kenako ananama kuti: “Kufa simudzafa ayi.” Ndiyeno pofuna kukopa Hava kuti asamvere Mulungu anamuuza kuti: “Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu.” Apa ankatanthauza kuti Yehova akuwamana zipatsozo podziwa kuti ziwathandiza kukhala ozindikira. Pomaliza anawalonjeza zinthu zabodza kuti: “Mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” w17.02 1:8, 9

Lachinayi, December 27

Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati panu, kuchokera pakati pa abale anu, ndipo inu mudzamvere mneneri ameneyo.​—Deut. 18:15.

Yesaya ananena kuti wosankhidwayo adzakhala “mtsogoleri ndi wolamulira.” (Yes. 55:4) Pomwe Danieli analemba zoti kudzabwera “Mesiya Mtsogoleri.” (Dan. 9:25) Ndiyeno Yesu mwiniwake ananena kuti iyeyo ndi “Mtsogoleri” wa anthu a Mulungu. (Mat. 23:10) Ophunzira ake ankamutsatira ndi mtima wonse ndipo sankakayikira zoti ndi wosankhidwa ndi Mulungu. (Yoh. 6:68, 69) Kodi n’chiyani chinkawatsimikizira? Pamene iye ankabatizidwa, Yohane anaona “kumwamba kukutseguka, ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera.” (Maliko 1:10-12) Kenako mzimu woyera unkathandiza Yesu kuti azichita zodabwitsa komanso kulankhula ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu. (Mac. 10:38) Unathandizanso Yesu kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chimwemwe ndiponso chikhulupiriro cholimba. (Yoh. 15:9; Aheb. 12:2) Palibe mtsogoleri wina amene ankachita zinthu ngati Yesu. N’zosachita kufunsa kuti Yesu anasankhidwadi ndi Yehova. w17.02 3:15, 16

Lachisanu, December 28

Kumbukirani amene akutsogolera pakati panu.​—Aheb. 13:7.

Pa Pentekosite mu 33 C.E., atumwi anayamba kutsogolera mpingo wachikhristu. Pa mwambowu, “Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja” ndipo analalikira kwa Ayuda ndi anthu amene analowa Chiyuda omwe anasonkhana. (Mac. 2:14, 15) Ambiri mwa anthuwo anakhala okhulupirira. Ndiyeno Akhristu atsopanowo “anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” (Mac. 2:42) Atumwi ankayang’anira ndalama za mpingo. (Mac. 4:34, 35) Ankasamaliranso anthu a Mulungu mwauzimu ndipo ananena kuti: “Ife tidzipereka ndithu pa kupemphera ndi pa utumiki wokhudza mawu a Mulungu.” (Mac. 6:4) Ndiponso anasankha Akhristu ena odalirika n’kuwapatsa ntchito yoti azikalalikira m’magawo atsopano. (Mac. 8:14, 15) Kenako, Akhristu ena odzozedwa anayamba kuthandiza atumwi posamalira mipingo. Iwo anali bungwe lolamulira limene linkapereka malangizo ku mipingo yonse.​—Mac. 15:2. w17.02 4:4

Loweruka, December 29

Perekani kwa onse zimene amafuna. . . . Amene amafuna kupatsidwa ulemu, m’patseni ulemu wake.—Aroma 13:7.

N’zosavuta kwa anthu ochimwafe kuti tiyambe kutengera mzimu wa dziko la Satanali. N’chifukwa chake anthu ambiri, m’malo mopereka ulemu woyenera kwa munthu, amayamba kum’patsa ulemu wofanana ndi kumulambira. Amalemekeza kwambiri atsogoleri achipembedzo ndi andale, akatswiri amasewera ndi azisudzo komanso anthu ena otchuka ndipo amawaona kuti ndi apamwamba kwambiri. Choncho amafuna atakhala ngati iwowo ndipo amatsanzira khalidwe lawo, kavalidwe kawo komanso zochita zawo. Koma Akhristu oona sapereka ulemu wosayenera kwa anthu. Khristu yekha ndi yemwe anali munthu wangwiro ndipo ndi amene tiyenera kumutsanzira. (1 Pet. 2:21) Mulungu sangasangalale tikamapereka ulemu wonyanyira kwa anthu. Tiyenera kukumbukira kuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Choncho palibe munthu amene ayenera kupatsidwa ulemu wofanana ndi kumulambira. w17.03 1:6-8

Lamlungu, December 30

Asa anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu masiku ake onse.​—1 Maf. 15:14.

Tonsefe tiyenera kufufuza mtima wathu kuti tione ngati timatumikira Mulungu modzipereka. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimafunitsitsa kusangalatsa Yehova, kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera komanso kuteteza anthu a Mulungu ku zinthu zoipa?’ Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati wachibale kapena mnzanu wachita tchimo koma sanalape ndipo wachotsedwa mumpingo? Kodi mungalimbe mtima n’kusiya kuchita naye zinthu? Kodi mtima wanu ungakulimbikitseni kutsatira malangizo a Mulungu? Mofanana ndi Asa tingasonyezenso kuti timatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu ngati timamudalira anthu ena akamatitsutsa. Mwina anzanu akusukulu angamakunyozeni chifukwa choti ndinu wa Mboni za Yehova. Kapena anzanu akuntchito angamaone kuti simuganiza bwino mukamapempha tchuthi kuti mukakhale nawo pamsonkhano kapena mukamakana kugwira ovataimu. Zikatere, muzipemphera kwa Mulungu ngati mmene Asa anachitira. (2 Mbiri 14:11) Muziyesetsanso kuchita zomwe mukudziwa kuti n’zoyenera. Muzikumbukira kuti Mulungu anathandiza Asa ndipo angakuthandizeninso inuyo. w17.03 3:6-8

Lolemba, December 31

Aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.​—Miy. 21:5.

Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tisamasankhe zochita mopupuluma pa nkhani zikuluzikulu. Tikaganizira mfundo zosiyanasiyana tisanasankhe zochita, tikhoza kusankha zinthu mwanzeru. (1 Ates. 5:21) Amuna asanasankhe zochita pa nkhani yokhudza banja lonse ayenera kufufuza m’Malemba, m’mabuku athu komanso kumva maganizo a anthu ena m’banjamo. Kumbukirani kuti Yehova anauza Abulahamu kuti amvere maganizo a mkazi wake. (Gen. 21:9-12) Nawonso akulu ayenera kufufuza asanasankhe zochita. Iwo ayenera kukhala ololera komanso odzichepetsa. Makhalidwewa angawathandize kuti akadziwa mfundo zatsopano, asamaope kusintha zimene anasankha poganiza kuti anyozeka. Iwo ayenera kukhala okonzeka kusintha ngati pakufunika kutero, ndipo ifenso tiyenera kutengera chitsanzo chawo. Izi zingathandize kuti mumpingo mukhale bata ndi mtendere.​—Mac. 6:1-4. w17.03 2:16

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena