Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 57-67
  • June

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • June
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Loweruka, June 1
  • Lamlungu, June 2
  • Lolemba, June 3
  • Lachiwiri, June 4
  • Lachitatu, June 5
  • Lachinayi, June 6
  • Lachisanu, June 7
  • Loweruka, June 8
  • Lamlungu, June 9
  • Lolemba, June 10
  • Lachiwiri, June 11
  • Lachitatu, June 12
  • Lachinayi, June 13
  • Lachisanu, June 14
  • Loweruka, June 15
  • Lamlungu, June 16
  • Lolemba, June 17
  • Lachiwiri, June 18
  • Lachitatu, June 19
  • Lachinayi, June 20
  • Lachisanu, June 21
  • Loweruka, June 22
  • Lamlungu, June 23
  • Lolemba, June 24
  • Lachiwiri, June 25
  • Lachitatu, June 26
  • Lachinayi, June 27
  • Lachisanu, June 28
  • Loweruka, June 29
  • Lamlungu, June 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 57-67

June

Loweruka, June 1

Mulungu ndiye chikondi.—1 Yoh. 4:16.

Yehova amatiphunzitsa, kutilangiza komanso kupereka chilango n’cholinga choti tipitirize kukhala naye pa ubwenzi komanso kuti tidzalandire moyo wosatha. Amachita zonsezi chifukwa chakuti amatikonda. Koma nthawi zina munthu akhoza kupatsidwa chilango osati kungolangizidwa. Mwachitsanzo, ngati munthu wachita tchimo lalikulu akhoza kuletsedwa kuti asamachite zinthu zina mumpingo. Komabe zinthu ngati zimenezi nazonso zimasonyeza chikondi cha Mulungu. Munthu akaletsedwa kuchita zinthu zina mumpingo, akhoza kuzindikira kufunika kokhala ndi nthawi yambiri yophunzira Baibulo, kusinkhasinkha komanso kupemphera. Zimenezi zingamuthandize kuti akhale wolimba mwauzimu. (Sal. 19:7) Pakapita nthawi, akhoza kuuzidwa kuti ayambirenso kuchita zimene analetsedwazo. Kuchotsa munthu mumpingo kumasonyezanso chikondi cha Yehova chifukwa mpingo umakhala wotetezeka. (1 Akor. 5:6, 7, 11) Mulungu amapereka chilango kwa munthu mogwirizana ndi zimene walakwitsa. Choncho munthu akachotsedwa mumpingo amatha kuzindikira kuti tchimo lake ndi lalikulu kwambiri ndipo akufunika kulapa.​—Mac. 3:19. w18.03 24 ¶5-6

Lamlungu, June 2

Iye ndi a m’banja lake, anabatizidwa mosataya nthawi.​—Mac. 16:33.

Woyang’anira ndendeyo sankadziwa Malemba. Iye ankafunika kuphunzira mfundo zoyambirira za m’Baibulo, kuzindikira zimene atumiki a Mulungu ayenera kuchita komanso kukhala ndi mtima wofuna kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa. Pa kanthawi kochepa chabe, mfundo zimene anaphunzira zinamufika pa mtima ndipo ankafuna kubatizidwa. (Mac. 16:25-33) N’zosachita kufunsa kuti atabatizidwa anapitiriza kuphunzira mfundo zina za m’Malemba. Ndiye poganizira zimene zinachitikira banjali, kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwana wanu akusonyeza kuti amakonda mfundo zoyambirira za m’Baibulo komanso akumvetsa bwino tanthauzo la kudzipereka komanso kubatizidwa? Mwina mungamulimbikitse kuti akaonane ndi akulu kuti akambirane naye n’kuona ngati akuyenerera ubatizo. Mofanana ndi Akhristu ena onse obatizidwa, iye adzapitiriza kuphunzira za Yehova ndiponso za cholinga chake mpaka muyaya.​—Aroma 11:33, 34. w18.03 10 ¶8-9

Lolemba, June 3

[Mukhale] ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.—Aroma 15:5.

Tikamachita khama kuti tikule mwauzimu, mzimu woyera umatipatsa mphamvu kuti tisinthe maganizo athu. Pang’ono ndi pang’ono timayamba kukhala ndi maganizo amene Khristu anali nawo. Mzimu ungatithandizenso kuti tisiye kulakalaka zinthu zoipa n’kumakhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu. Kukhala ndi maganizo a Khristu kungatithandize kuti zolankhula zathu ndiponso zochita zathu kusukulu kapena kuntchito zizikhala zabwino. Kungatithandizenso kuti tizisankha zinthu mwanzeru tsiku lililonse. Ndipo zimene tingasankhe zingasonyeze kuti timatsatiradi Khristu. Munthu amene ali ndi maganizo a Khristu salola kuti chilichonse chisokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Akakumana ndi mayesero, chimene chimabwera m’mutu mwamsanga ndi kukana. Asanasankhe zochita amayamba wadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene ingandithandize kusankha bwino? Kodi akanakhala Khristu akanatani pamenepa? Nanga ndi ziti zimene ndingasankhe kuti ndisangalatse Yehova?’ w18.02 25 ¶12; 26 ¶14

Lachiwiri, June 4

Nowa anayanjidwa ndi Yehova.​—Gen. 6:8.

Mu nthawi ya Inoki, yemwe anali agogo a bambo a Nowa, anthu anali atalowerera kwambiri. Iwo anafika ponena ‘zinthu zonyoza kwambiri’ Yehova. (Yuda 14, 15) Zachiwawa zinkawonjezerekawonjezereka moti munthawi ya Nowa dziko lapansi “linadzaza ndi chiwawa.” Angelo oipa anabwera padziko n’kumakhala ngati anthu, anakwatira ndipo anabereka ana ankhanza kwambiri. (Gen. 6:2-4, 11, 12) Koma Nowa anali wosiyana kwambiri ndi anthu ena.“Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.” (Gen. 6:8, 9) Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu amenewa? Choyamba, sikuti Nowa anangoyenda ndi Mulungu m’dziko loipalo kwa zaka 70 kapena 80 zokha, zomwe anthu amakhala ndi moyo masiku ano. Iye anakhala m’dziko loipalo kwa zaka pafupifupi 600. (Gen. 7:11) Komanso mosiyana ndi ifeyo, Nowa analibe mpingo wa abale ndi alongo amene akanamulimbikitsa. Zikuonekanso kuti ngakhale azibale ake sankamulimbikitsa. w18.02 4 ¶4-5

Lachitatu, June 5

Anthu adzakhala . . . okonda ndalama,​—2 Tim. 3:2.

Anthu okonda ndalama sakhutira ndi zimene ali nazo ndipo akamayesetsa kuti alemere, ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri.’ (1 Tim. 6:9, 10; Mlal. 5:10) N’zoona kuti tonsefe timafunikira ndalama. Zili choncho chifukwa zimatiteteza m’njira zina. (Mlal. 7:12) Koma funso n’lakuti, Kodi n’zotheka munthu amene amangopeza zofunika pa moyo zokha kukhaladi wosangalala? Inde. (Mlal. 5:12) Aguri mwana wa Yake anapempha Mulungu kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya.” M’pomveka kuti sankafuna kukhala mphawi wadzaoneni. Iye anafotokoza kuti sankafuna zimenezi chifukwa zikhoza kumuchititsa kuti abe n’kunyozetsa Mulungu. Koma n’chifukwa chiyani sankafuna kukhala ndi chuma? Iye anapitiriza kuti: “Kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani kuti: ‘Kodi Yehova ndani?’” (Miy. 30:8, 9) Yesu ananena kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Mat. 6:24. w18.01 24 ¶9-11

Lachinayi, June 6

Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.​—Mat. 18:35.

Timagwirizana tikamakhala ndi mtima wokhululukira ena. Tikamakhululukira anzathu, timasonyeza kuti timayamikira nsembe ya dipo imene Khristu anapereka yomwe imathandiza kuti nafenso machimo athu akhululukidwe. Fanizo limene Yesu ananena pa Mateyu 18:23-34 lingatithandize kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani yokhululuka. Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimayesetsa kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa? Kodi ndimamvetsa Akhristu anzanga komanso kuwalezera mtima? Kodi ndine wokonzeka kukhululukira munthu aliyense amene angandilakwire?’ N’zoona kuti machimo ena amakhala aakulu moti zingavute kuti munthu yemwe si wangwiro awaiwale. Koma fanizoli likutithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani yokhululukayi. Yesu ananena momveka bwino kuti Yehova sadzatikhululukira ngati ifeyo timakana kukhululukira anzathu pamene pali zifukwa zowakhululukira. Mfundo imeneyitu ndi yofunika kuiganizira kwambiri. Tikamayesetsa kutsatira malangizo a Yesu akuti tizikhululukira anzathu timathandiza kuti tizigwirizana kwambiri. w18.01 15 ¶12

Lachisanu, June 7

Mukhazikitse lamulo loletsa munthu aliyense kupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kupatulapo kwa inu nokha mfumu. Aliyense amene samvera lamulo limeneli aponyedwe m’dzenje la mikango.​—Dan. 6:7.

Danieli analolera kuika moyo wake pa ngozi n’kupitiriza kupemphera poyera chifukwa sankafuna kuti anthu aganize zoti wasiya kutumikira Yehova. Yehova anadalitsa Danieli chifukwa choti analimba mtima ndipo anamupulumutsa modabwitsa kuti asaphedwe ndi mikango. Ndipotu zimenezi zinachititsa kuti anthu a mu ufumu wonse wa Amedi ndi Aperisiya adziwe za Yehova. (Dan. 6:25-27) Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Danieli? Kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, chofunika si kungowerenga Mawu a Mulungu koma “kuzindikira tanthauzo lake.” (Mat. 13:23) Tiyenera kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo kuti tizidziwa bwino maganizo a Yehova. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuganizira kwambiri zimene timawerenga m’Baibulo. Tiyeneranso kupemphera kuchokera pansi pa mtima, makamaka tikamakumana ndi mayesero kapena mavuto. Tikamapempha Mulungu mwachikhulupiriro kuti atipatse nzeru ndiponso mphamvu, adzatipatsadi mowolowa manja.​—Yak. 1:5. w18.02 10-11 ¶13-15

Loweruka, June 8

Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.​—Sal. 34:8.

Ngakhale achinyamata amaona ubwino wa Yehova akamawathandiza kulalikira, kaya ali mu utumiki kapena kusukulu. Anthu ena amavutika kulalikira kwa anzawo kusukulu, ndipo n’zomveka chifukwa sadziwa kuti anzawowo angachite chiyani. Komanso zimavuta kwambiri kulankhula ndi gulu kusiyana ndi kulankhula ndi munthu mmodzi. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Choyamba muyenera kuganizira zimene zimakutsimikizirani kuti zomwe mumakhulupirira ndi zolondola. Ngati nkhani zapawebusaiti yathu zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” zilipo m’chilankhulo chanu, muyenera kuzigwiritsa ntchito. Nkhani zimenezi zikhoza kukuthandizani kuganizira mfundo zimene mumakhulupirira, kutsimikizira kuti n’zolondola komanso kuti muzitha kuzifotokoza kwa anthu ena. Mukatsimikizira mfundozo n’kuzikonzekera bwino, mudzakhala ofunitsitsa kuuza ena za Yehova.​—Yer. 20:8, 9. w17.12 26 ¶12, 14-15

Lamlungu, June 9

Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo.​—2 Tim. 3:14.

Kuti mwana ayambe kukonda Yehova pamafunika zambiri osati kungodziwa nkhani kapena anthu otchulidwa m’Baibulo. Paja tanena kale kuti Timoteyo ‘anakhulupirira zinthu pambuyo pokhutira nazo.’ M’Chigiriki, mawu amenewa amatanthauza kuti “anatsimikiziridwa” kapena kuti “anapeza umboni wakuti ndi zoona.” Timoteyo ankadziwa Malemba Achiheberi kuyambira ali wakhanda. Koma kenako iye anapeza umboni womutsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya. Kodi inuyo mungathandize bwanji ana anu kuti akhale ndi chikhulupiriro ngati cha Timoteyo? Choyamba muyenera kukhala oleza mtima. Chikhulupiriro choterechi sichingayambe lero ndi lero ndipo ana anu sangayambe kukhulupirira zinthu chifukwa choti inuyo mumazikhulupirira. Mwana aliyense amafunika kugwiritsa ntchito luso lake la kuganiza kuti ayambe kukhulupirira mfundo za m’Baibulo? (Aroma 12:1) Ndiyeno inuyo monga makolo muli ndi udindo wothandiza ana anu pa nkhaniyi, makamaka ngati akukufunsani zinazake. w17.12 19 ¶3, 5-6

Lolemba, June 10

Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.—Yoh. 11: 24.

Lazaro atamwalira, Marita anali ndi chisoni kwambiri. Iye anali wophunzira wa Yesu komanso mnzake ndipo Yesuyo anamutonthoza pomuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.” (Yoh. 11:20-23) Marita sankakayikira kuti m’tsogolomu Lazaro adzauka. Kenako Yesu anachita zinthu zodabwitsa kwambiri chifukwa anaukitsa Lazaro tsiku lomwelo. Masiku ano sitiyembekezera kuti Yesu kapena Atate wake angatichitire zomwezo. Koma kodi inuyo mumakhulupiriranso ndi mtima wonse kuti m’tsogolo akufa adzauka? Mwina munthu wina amene munkamukonda kwambiri anamwalira ndipo mukulakalaka mutamuona, kucheza naye kapena kumukumbatira. N’kutheka kuti amene anamwalira ndi mwamuna kapena mkazi wanu, mayi anu, bambo anu, agogo anu kapenanso mwana wanu. N’zosangalatsa kuti mofanana ndi Marita, muli ndi zifukwa zomveka zoti munenenso kuti: ‘Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa.’ Ndi bwino kuti Mkhristu aliyense aziganizira zifukwa zimene zingatichititse kuti tisamakayikire zoti akufa adzauka. w17.12 3 ¶1-2

Lachiwiri, June 11

Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.​—Sal. 40:8.

Yesu ankakonda kwambiri Chilamulo cha Mose. Izi n’zosadabwitsa chifukwa amene anapereka Chilamulocho ndi Atate wake, omwe ndi ofunika kwambiri kuposa aliyense. Lemba la lero linalosera kuti Yesu azidzakonda malamulo a Mulungu. Zolankhula komanso zochita za Yesu zinkasonyeza kuti iye amaona kuti Chilamulo cha Mulungu ndi changwiro, chothandiza komanso sichingalephere kukwaniritsidwa. (Mat. 5:17-19) Yesu ayenera kuti zinamuwawa kwambiri kuona alembi ndi Afarisi akupotoza Chilamulo cha Atate wake. Iye ananena kuti iwo ankatsatira tizigawo ting’onoting’ono ta Chilamulocho n’kumanyalanyaza mfundo zofunika kwambiri ndipo anawauza kuti: “Mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.” (Mat. 23:23) Mosiyana ndi anthu okhwimitsa zinthuwa, Yesu ankadziwa bwino cholinga cha Chilamulo komanso mfundo zokhudza Mulungu zimene tingaphunzire pa lamulo lililonse. w17.11 13 ¶1-2

Lachitatu, June 12

Mulungu akufuna kuti mukhale oyera mwa kupewa dama.—1 Ates. 4:3.

Anthu akhoza kutiuza kuti: “Anthufe timafunika kusangalala ndi moyo. Ndiye cholakwika n’chiyani ngati anthu amene sali pa banja atagonana?” Si nzeru kuganiza kuti zimenezi zilibe vuto lililonse. Tikutero chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amaletsa chiwerewere. (1 Ates. 4:4-8) Yehova ndi amene anatilenga, choncho ali ndi ufulu wotipatsa malamulo. Malamulo a Mulungu amanena kuti mwamuna ndi mkazi akhoza kugonana pokhapokha ngati ali pa banja. Mulungu amatipatsa malamulo chifukwa chotikonda ndipo amadziwa kuti malamulowo ndi othandiza. Mabanja amene amatsatira malamulowa amakhala okondana, aulemu komanso otetezeka. Mulungu salekerera anthu amene satsatira mwadala malamulo ake. (Aheb. 13:4) Mawu a Mulungu amatipatsa malangizo othandiza kuti tizipewa chiwerewere. Njira imodzi yofunika kwambiri ndi kusamala ndi zimene timaona. (Mat. 5:28, 29) Choncho Akhristu amapewa kuonera zolaula kapena kumvetsera nyimbo zolimbikitsa chiwerewere.​—Aef. 5:3-5. w17.11 22 ¶9-10

Lachinayi, June 13

Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.—Sal. 147:1.

Kuyambira kalekale, atumiki okhulupirika a Yehova akhala akuimba nyimbo pomutamanda. Chochititsa chidwi n’chakuti pamene Aisiraeli ankalambira Yehova mokhulupirika, kuimba nyimbo zotamanda Yehova kunkakhalanso kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, pokonzekera utumiki umene unkachitika kukachisi, Davide anakonza zoti pakhale Alevi 4,000 oimba nyimbo zotamanda Yehova. Ndipo pa anthu amenewa, anthu 288 anali ‘akatswiri ophunzitsidwa kuimbira Yehova.’ (1 Mbiri 23:5; 25:7) Pamwambo wotsegulira kachisi, panaimbidwa nyimbo zambiri. Baibulo limanena kuti: ‘Anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwirizana n’kumamveka ngati mawu amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova. Komanso anayamba kuimba ndi malipenga, zinganga, ndi zoimbira zina potamanda Yehova ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.’ Zimenezi ziyenera kuti zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Aisiraeliwo.​—2 Mbiri 5:13, 14; 7:6. w17.11 4 ¶4-5

Lachisanu, June 14

Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere koma lupanga.​—Mat. 10:34.

Yesu ankadziwa kuti zimene ankaphunzitsa zingagawanitse anthu, ndiponso kuti anthu amene amamutsatira ayenera kukhala olimba mtima chifukwa azitsutsidwa. Cholinga cha Yesu chinali kulengeza uthenga wochokera kwa Mulungu, osati kugawanitsa anthu. (Yoh. 18:37) Komabe kutsatira mokhulupirika zimene ankaphunzitsa kungakhale kovuta ngati achibale komanso anzake a munthuyo ali osakhulupirira. Kuti asonyeze kuti ndi Akhristu enieni, otsatira a Yesu amapirira akamanyozedwa kapena kusalidwa ndi achibale awo. Komabe amapeza madalitso ambiri oposa zimene ataya. (Maliko 10:29, 30) Achibale athu akamatitsutsa, timapitirizabe kuwakonda. Komabe tizikumbukira kuti tiyenera kukonda Yehova ndi Khristu kuposa achibalewo. (Mat. 10:37) Tizikumbukiranso kuti Satana angagwiritse ntchito chikondi chimene timakhala nacho pa achibale athu kuti atichititse kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. w17.10 13 ¶3-6

Loweruka, June 15

Anamukankha [Kuipa] n’kumubwezera m’chiwiya choyezera chokwana muyezo wa efacho, ndipo anavundikira chiwiyacho ndi chivundikiro chake chamtovu chija.​—Zek. 5:8.

Masomphenya amenewa akusonyeza kuti Yehova sadzalekerera kuipa kwa mtundu uliwonse pakati pa anthu ake. Iye adzaonetsetsa kuti kuipako kwasamaliridwa n’kuchotsedwa mwamsanga. (1 Akor. 5:13) Zimene mngelo uja anachita povundikira chiwiya chija mwamsanga zikutsimikizira mfundo imeneyi. Masomphenya amenewa ayenera kuti anawakhazika mtima pansi Aisiraeli a nthawi ya Zekariya chifukwa anawatsimikizira kuti Yehova sadzalekerera anthu ofuna kuipitsa kulambira koyera. Komabe masomphenyawa anakumbutsanso Ayuda kuti ayenera kuyesetsa kuti kulambira kwawo kuzikhala koyera nthawi zonse. Anthu a Yehova sayenera kulola kuti zinthu zoipa zilowe m’gulu lawo n’kukhazikika. Yehova watilola kuti tikhale m’gulu lake loyera limene limatisamalira mwachikondi choncho tili ndi udindo woonetsetsa kuti gululi lipitirizebe kukhala loyera. Kodi ifeyo timayesetsa kuchita zimenezi? M’paradaiso wathu wauzimu simuyenera kupezeka kuipa kwa mtundu uliwonse. w17.10 24 ¶14-15; 25 ¶17-18

Lamlungu, June 16

Ndimakonda chilamulo chanu.—Sal. 119:163.

Mabuku 39 oyambirira a m’Baibulo analembedwa ndi Aisiraeli kapena kuti Ayuda. Paja Baibulo limanena kuti poyamba “mawu opatulika a Mulungu anaikidwa m’manja mwa Ayuda.” (Aroma 3:1, 2) Koma pofika m’ma 200 B.C.E., Ayuda ambiri sankamva Chiheberi. Zinali choncho chifukwa choti ulamuliro wa Agiriki unafalikira m’madera ambiri nthawi ya Alekizanda Wamkulu. (Dan. 8:5-7, 20, 21) Zimenezi zinachititsa kuti Chigiriki chikhale chilankhulo chodziwika ndi anthu ambiri, kuphatikizapo Ayuda amene ankakhala m’madera amenewa. Ayuda ambiri atayamba kulankhula Chigiriki ankavutika kumva Malemba Achiheberi. Kodi vuto limeneli linatha bwanji? Malemba Achiheberi anamasuliridwa m’Chigiriki ndipo ntchitoyi inamalidzidwa m’ma 100 B.C.E., mabuku ena amene anatsala m’Malemba Achiheberi anali atamasuliridwanso m’Chigiriki. Ataphatikiza mabuku onse a Malemba Achiheberi omasuliridwa m’Chigiriki, anapanga Baibulo lomwe limadziwika kuti Septuagint. Limeneli linali Baibulo loyamba kumasulira Malemba onse Achiheberi m’Chigiriki. w17.09 20 ¶7-9

Lolemba, June 17

Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.​—Aheb. 13:5.

Abwana anu akhoza kukupemphani kuti muzigwira ntchito nthawi imene mumakalalikira, kusonkhana kapena kuchita kulambira kwa pabanja. Mumafunika kulimba mtima kuti mukane zimenezi n’kupereka chitsanzo chabwino kwa ana anu. Pamafunikanso kulimba mtima kuti tithandize ana athu kuti asankhe kuchita zambiri potumikira Yehova. Mwachitsanzo, makolo ena amaopa kulimbikitsa ana awo kuti ayambe upainiya, apite kukatumikira kumene kukufunika ofalitsa ambiri, akatumikire ku Beteli kapena akagwire nawo ntchito zomanga Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano. Mwina amaona kuti anawo akachita zimenezi sadzakwanitsa kuwasamalira akadzakalamba. Koma makolo anzeru amakhala olimba mtima n’kumakhulupirira zimene Yehova walonjeza. (Sal. 37:25) Makolo amene amalimba mtima n’kumadalira Yehova amathandiza ana awo kuti azichitanso zomwezo.​—1 Sam. 1:27, 28; 2 Tim. 3:14, 15. w17.09 30 ¶14-15

Lachiwiri, June 18

Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo . . . kudziletsa.​—Agal. 5:22, 23.

Ngati ndinu makolo, kodi mungathandize bwanji ana anu kuti akhale odziletsa? Muyenera kudziwa kuti ana sabadwa ndi mtima wodziletsa. Pophunzitsa ana anu makhalidwe abwino, muyenera kupereka chitsanzo chabwino. (Aef. 6:4) Choncho mukaona kuti ana anu akuvutika kudziletsa, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikupereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi?’ Dziwaninso kuti chitsanzo chanu chabwino pa nkhani yolalikira, kusonkhana komanso kuchititsa kulambira kwa pabanja chingathandize kwambiri ana anu. Mwana wanu akapempha zinthu zimene mukuona kuti sizingamuthandize musamaope kumukaniza. Paja nayenso Yehova analetsa Adamu ndi Hava kuchita zinthu zina n’cholinga choti azizindikira komanso kulemekeza ulamuliro wake. Makolo akamalangiza ana awo komanso kupereka chitsanzo chabwino akhoza kuthandiza anawo kuti akhale odziletsa. Kukonda Mulungu komanso kulemekeza malamulo ake ndi zinthu zofunika kwambiri zimene makolo ayenera kuphunzitsa ana awo.​—Miy. 1:5, 7-8. w17.09 7 ¶17

Lachitatu, June 19

Thupi lisakhale logawanika, koma ziwalo zake zisamalirane mofanana.​—1 Akor. 12:25.

Anthufe tizikumanabe ndi mavuto mpaka dziko la Satanali litawonongedwa. Tikhoza kuvutika ndi matenda, kuzunzidwa, ngozi zadzidzidzi, kusowa ntchito, kuberedwa komanso mavuto ena. Kuti tikwanitse kuthandizana pa mavuto ngati amenewa, tiyenera kukhala anthu achifundo. Chifundo chachikulu chingatilimbikitse kuti tikhale anthu okoma mtima. (Aef. 4:32) Makhalidwe awiriwa angatithandize kuti tizitsanzira Mulungu komanso tizilimbikitsa anthu ena. (2 Akor. 1:3, 4) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira anthu ochokera m’mayiko ena kapena anthu ovutika mumpingo? Tiyenera kucheza nawo ndiponso kuwathandiza kuona kuti ndi ofunika kwambiri mumpingo. (1 Akor. 12:22) Abale ndi alongo ambiri amachitira chifundo anthu ochokera m’mayiko ena moti amaphunzira chilankhulo chawo ndipo zotsatira zake ndi zabwino kwambiri.​—1 Akor. 9:23. w17.08 23-24 ¶7-9

Lachinayi, June 20

Yehova ndiye cholowa changa. Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.—Maliro 3:24.

Tonsefe tiyenera kukhala oleza mtima n’kumayembekezera Yehova. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake. Tizikumbukira kuti kuleza mtima ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Aef. 3:16; 6:18; 1 Ates. 5:17-19) Choncho tiyenera kuchonderera Yehova kuti atithandize kupirira moleza mtima. Tizikumbukiranso zimene zinathandiza Abulahamu, Yosefe komanso Davide kuti aziyembekezera malonjezo a Yehova moleza mtima. Iwo ankakhulupirira kwambiri Yehova ndiponso kukumbukira zimene anawachitira. Sankangoganizira zimene ankafuna pa moyo wawo. Kuganizira madalitso amene anthu amenewa anapeza chifukwa choleza mtima kungatithandize kuti nafenso tiziyembekezera moleza mtima. Choncho ngakhale kuti timakumana ndi mavuto, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi “mtima wodikira.” N’zoona kuti nthawi zina tingafunse kuti, “Mpaka liti, Yehova?” (Yes. 6:11) Koma mzimu woyera wa Mulungu ungatipatse mphamvu ndipo tingafune kunena mawu amene ali mulemba la lero. w17.08 7 ¶18-20

Lachisanu, June 21

Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.—Sal. 40:8.

N’zosachita kufunsa kuti Yesu ali mwana ankasewera ndiponso kusangalala. Paja Mawu a Mulungu amanena kuti pali “nthawi yoseka” ndi “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlal. 3:4) Koma Yesu ankakondanso kuphunzira Malemba n’cholinga choti alimbitse ubwenzi wake ndi Yehova. Iye ali ndi zaka 12 zokha, aphunzitsi akukachisi anadabwa kwambiri ndi ‘mayankho ake komanso poona kuti ankamvetsa kwambiri zinthu’ zokhudza Yehova. (Luka 2:42, 46, 47) Yesu atakula ankakhalanso wosangalala chifukwa chakuti ankakonda kuchita zimene Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, Mulungu ankafuna kuti iye azilengeza ‘uthenga wabwino kwa osauka komanso kuthandiza akhungu kuti ayambe kuona.’ (Luka 4:18) Yesu ankakonda kwambiri kuphunzitsa anthu zokhudza Atate wake wakumwamba. (Luka 10:21) Iye ataphunzitsa mayi wina anauza ophunzira ake kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yoh. 4:31-34) Yesu ankasonyeza kuti amakonda Mulungu komanso anthu ndipo izi zinkachititsa kuti azisangalala. Inunso mukhoza kukhala osangalala mukamachita zimenezi. w17.07 23 ¶4-5

Loweruka, June 22

Mtendere wa Mulungu . . . udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.​—Afil. 4:7.

Zimene Yesu ankalankhula komanso kuchita ali padzikoli zimasonyeza bwino chifundo cha Yehova. (Yoh. 5:19) Mulungu anatumiza Mwana wakeyu padziko kuti alimbikitse “anthu osweka mtima” komanso atonthoze “anthu onse olira.” (Yes. 61:1, 2; Luka 4:17-21) N’chifukwa chake iye anali wachifundo, ankamvetsa mavuto a anthu komanso ankafunitsitsa kuwathandiza. (Aheb. 2:17) Baibulo limanena kuti “Yesu Khristu ali chimodzimodzi dzulo ndi lero, ndiponso mpaka muyaya.” (Aheb. 13:8) Popeza Yesu yemwe ndi “Mtumiki Wamkulu wa moyo” amamvetsa mmene zimakhalira munthu akaferedwa, “amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.” (Mac. 3:15; Aheb. 2:10, 18) Khristu sanasiye kumvera chisoni anthu, kumvetsa mmene akumvera ndiponso kuwalimbikitsa ‘pa nthawi imene akufunika thandizo.’​—Aheb. 4:15, 16. w17.07 13 ¶6-7; 14 ¶10

Lamlungu, June 23

Kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.—Luka 12:34.

Satana ndi dziko loipali akhoza kutichititsa kuti tisiye kuyamikira chuma chimene takambirana munkhaniyi. N’zosavuta kutengeka chifukwa chofuna ntchito yabwino, moyo wawofuwofu komanso kudzionetsera ndi zinthu zimene tili nazo. Koma mtumwi Yohane anatichenjeza kuti dzikoli likupita limodzi ndi chilakolako chake. (1 Yoh. 2:15-17) Choncho tiyenera kusamala kwambiri kuti tisayambe kukonda zinthu za m’dzikoli. M’malomwake, tiyeni tipitirize kukonda komanso kuyamikira chuma chimene Mulungu watipatsa. Tiyeni tizipewa chilichonse chimene chingatilepheretse kukonda kwambiri Ufumu wa Mulungu. Tizilalikira modzipereka ndiponso tisasiye kuona kuti utumiki wathu ndi wofunika kwambiri. Tiyeneranso kupitiriza kufufuza mwakhama mfundo za m’Baibulo. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikusunga ‘chuma chosatha kumwamba, kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete singawononge.’​—Luka 12:33. w17.06 13 ¶19-20

Lolemba, June 24

Kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.​—Sal. 84:10.

Yehova salamulira mopondereza ndipo si womva zake zokha. Iye anapereka ufulu kwa anthu ndipo izi zimathandiza kuti anthu azisangalala. (2 Akor. 3:17) Pa nkhani imeneyi, Davide analemba kuti: “Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake [pa Mulungu], pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.” (1 Mbiri 16:7, 27) Nayenso Etani, amene analemba masalimo ena, anati: “Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala. Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova. Iwo amakondwera ndi dzina lanu tsiku lonse. Chilungamo chanu chimawakweza.” (Sal. 89:15, 16) Tikamaganizira zinthu zabwino zimene Yehova amachita timatsimikizira kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Maganizo amenewa ndi omveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga komanso amadziwa zimene zingatisangalatse ndipo amatipatsa zinthuzo mowolowa manja. Chilichonse chimene amatiuza kuti tichite chimakhala chotithandiza ndipo tikamvera timasangalala. Izi zimachitika ngakhale pamene tiyenera kudzimana zinthu zina kuti timumvere.​—Yes. 48:17. w17.06 29 ¶10-11

Lachiwiri, June 25

Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.​—Miy. 13:12.

Pali mlongo wina wa ku England amene ankafunitsitsa atakhala ndi mwana koma sizinatheke. Kenako anafika msinkhu woti sangaberekenso. Iye ananena kuti anadandaula kwambiri atazindikira kuti sadzaberekanso mwana m’dziko lakaleli. Choncho iye ndi mwamuna wake anasankha kuti angopeza mwana woti azimulera ngati wawo. Komabe mlongoyo anati: “Zinkandiwawabe chifukwa ndinkadziwa kuti kulera mwana wa wina si kofanana ndi kulera mwana wakowako.” Baibulo limanena kuti akazi achikhristu ‘amatetezeka akabereka mwana.’ (1 Tim. 2:15) Izi sizikutanthauza kuti akabereka mwana amakhala ndi mwayi wopeza moyo wosatha. Zikungotanthauza kuti akamasamalira mwanayo komanso kugwira ntchito zina zapakhomo, sakhala ndi nthawi yolowerera nkhani za eni kapena kuchita miseche.​—1 Tim. 5:13. w17.06 5-6 ¶6-8

Lachitatu, June 26

Kodi mumam’patsa chiyani [Mulungu]? Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?—Yobu 35:7.

Kodi Elihu ankatanthauza kuti zimene timachita potumikira Mulungu n’zopanda ntchito? Ayi. Tikutero chifukwa Yehova sanamudzudzule ngati mmene anachitira ndi amuna atatu aja. Elihu ankatanthauza kuti Yehova ali ndi chilichonse ndipo samadalira zimene timachita pomulambira. Ifeyo sitingamuthandize kuti akhale wolemera kapena wamphamvu kuposa mmene alili. Iye ndi amene amatipatsa luso, mphamvu komanso zinthu zilizonse zabwino zimene tili nazo ndipo amaona mmene timazigwiritsira ntchito. Tikachitira zabwino Akhristu anzathu, Yehova amaona kuti tachitira iyeyo. Lemba la Miyambo 19:17 limati: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.” Lembali likutanthauza kuti Yehova amaona zabwino zilizonse zimene timachitira anthu ooneka ngati onyozeka. Ngakhale kuti iye ndi Mlengi wa chilengedwe chonse amadziwa zabwino zimene anthufe timachitira ena. Amaona kuti tamukongoza iyeyo ndipo adzatibwezera potidalitsa. Zimene Mwana wake ananena zimasonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona.​—Luka 14:13, 14. w17.04 29 ¶3-4

Lachinayi, June 27

Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.​—Sal. 1:2.

Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo komanso mabuku athu, kodi tingachitenso chiyani kuti tizikonda kwambiri choonadi? Tiyenera kupezeka pamisonkhano yonse yampingo. Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi njira yaikulu imene Yehova amatiphunzitsira. Koma kuti tizimvetsa bwino nkhani zake tiyenera kukonzekera bwino phunziro lililonse. Pokonzekera tiyenera kuwerenga malemba onse amunkhaniyo. Masiku ano, tikhoza kuchita dawunilodi Nsanja ya Olonda m’zilankhulo zosiyanasiyana pawebusaiti ya jw.org kapena kuiwerenga pogwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Library. Tikamawerenga pogwiritsa zipangizo zamakono timatha kutsegula malemba amene ali munkhaniyo mosavuta. Koma kaya tikugwiritsa njira iti powerenga magazini, tikamawerenga ndiponso kuganizira kwambiri malembawa timayamba kukonda kwambiri choonadi. w17.05 20 ¶14

Lachisanu, June 28

Chotero aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.​—Aroma 14:12.

Munthu akabatizidwa amafunika kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene analonjeza. Ndipo akadzipereka kwa Mulungu, ndiye kuti wadzipereka basi moti n’zosatheka kusintha. Munthu sanganene kuti watopa ndi kutumikira Yehova kapena kuchita zimene Mkhristu amayenera kuchita ndipo akufuna kusintha kuti asamaonedwenso ngati Mkhristu wodzipereka ndiponso wobatizidwa. Izi n’zosatheka chifukwa munthuyo anadzipereka kale kwa Yehova ndi mtima wonse. Ndipo akachita machimo aakulu, amayenera kuyankha kwa Yehova komanso kumpingo. Choncho ndi bwino kuti tiziyesetsa kuti ‘tisasiye chikondi chimene tinali nacho poyamba.’ Koma tizichita zinthu zimene zingapangitse Yesu kutiuza kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:4, 19) Tiyeni tiziyesetsa kukwaniritsa lonjezo lathu kuti tizisangalatsa Yehova. w17.04 6-7 ¶12-13

Loweruka, June 29

Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama.​—Deut. 32:4.

Pa nthawi ina Abulahamu anafunsa kuti: “Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?” (Gen. 18:25) Abulahamu anafunsa funsoli chifukwa choti sankakayikira kuti Yehova adzaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwachilungamo. Iye ankakhulupirira kuti Yehova sangaphe “munthu wolungama limodzi ndi woipa.” Abulahamu ankaona kuti Mulungu ndi wachilungamo ndipo ‘sangachite zimenezo.’ Iye sankakayikira zoti Yehova amaweruza mwachilungamo chifukwa chakuti Yehova ndi wachilungamo kuposa wina aliyense. Izi zikutanthauza kuti mfundo zake ndi zachilungamo ndipo amaweruza moyenera. Ndipotu Baibulo limanena kuti Yehova “amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.”​—Sal. 33:5. w17.04 18-19 ¶1-2

Lamlungu, June 30

Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.​—3 Yoh. 4.

Chitsanzo chabwino cha makolo chingathandize kwambiri ana kuti ayambe kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha. Ngati ndinu makolo, ana anu akamaona kuti ‘mukufunafuna ufumu choyamba’ nawonso amayamba kudalira Yehova kuti aziwathandiza kupeza zinthu zofunika. (Mat. 6:33, 34) Choncho ndi bwino kukhala moyo wosalira zambiri ndipo muzipewa ngongole. Muziika zinthu zokhudza kutumikira Yehova pamalo oyamba, osati chuma. Muziyesetsa kusangalatsa Yehova. Mukatero ndiye kuti mukufunafuna “chuma kumwamba” osati chuma cha m’dzikoli kapena “ulemerero wa anthu.” (Maliko 10:21, 22; Yoh. 12:43) Musamatanganidwe kwambiri mpaka kusowa nthawi yocheza ndi ana anu. Muziwauza kuti mumawayamikira akamaika Yehova pamalo oyamba m’malo mofunafuna ndalama zambiri kapena zinthu zimene zingachititse kuti iwowo kapena banja lanu litchuke. Musamakhale ndi maganizo oti ana ayenera kufunafuna ndalama n’cholinga choti inuyo mudzakhale ndi moyo wawofuwofu. Muzikumbukira mfundo yakuti, “ana sayenera kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo m’tsogolo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira ana awo.”​—2 Akor. 12:14. w17.05 9 ¶3-4

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena