May
Lachitatu, May 1
Gwira malangizo, usawataye. Uwasunge bwino chifukwa iwo ndiwo moyo wako.—Miy. 4:13.
N’zoona kuti chilango chimapweteka, koma pali chinthu china chopweteka kwambiri kuposa chilango. Chinthu chake ndi mavuto amene amabwera chifukwa chosamvera malangizo. (Aheb. 12:11) Kuti timvetse mfundoyi, tiyeni tikambirane chitsanzo cha Kaini. Kaini atakwiya n’kumafuna kupha m’bale wake, Yehova anamulangiza kuti: “N’chifukwa chiyani wapsa mtima choncho, ndipo nkhope yako yagweranji? Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Kaini sanamvere malangizowa moti uchimo unamugonjetsa. Ndipo zotsatira zake zinali zopweteka kwambiri kuposa mmene anamupwetekera malangizo amene Yehova anamupatsa. (Gen. 4:11, 12) Yehova safuna kuti ifeyo tikumane ndi zinthu zopweteka ngati zimenezi. (Yes. 48:17, 18) Choncho tiyeni ifeyo ‘tizimvera malangizo kuti tikhale anzeru.’—Miy. 4:13. w18.03 32 ¶18-20
Lachinayi, May 2
Ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka . . . mwa kuwerenga mawu . . . olembedwa m’mabuku.—Dan. 9:2.
Danieli ayenera kuti anaphunzitsidwa bwino ndi makolo ake kuti azikonda Yehova komanso Mawu ake ndipo sanasinthe kwa moyo wake wonse. Iye ankakonda kuphunzira Malemba ngakhale atakalamba. Pemphero la Danieli lochokera pansi pa mtima limene lili pa Danieli 9:3-19 limasonyeza kuti ankadziwa bwino Yehova komanso mmene ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. Mungachite bwino kupeza mpata wowerenga pempheroli n’kuliganizira mofatsa kuti mudziwe zambiri zokhudza Danieli. Moyo wa ku Babulo unali wovuta kwambiri kwa Ayuda okhulupirika. Mwachitsanzo, Yehova anauza Ayuda kuti: “Mzinda umene ndakuchititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunira mtendere.” (Yer. 29:7) Koma pa nthawi imodzimodziyo Yehova ankafuna kuti Ayudawo azilambira iye yekha. (Eks. 34:14) Ndiye kodi n’chiyani chinathandiza Danieli kuti azichita zonsezi bwinobwino? Nzeru yochokera kwa Mulungu inamuthandiza kuti azilemekeza olamulira koma mosapitirira malire. Patapita zaka zambiri, Yesu anaphunzitsanso anthu mfundo yomweyi.—Luka 20:25. w18.02 10 ¶11-12
Lachisanu, May 3
Ulembe chizindikiro pamphumi za anthu.—Ezek. 9:4.
Kodi mukukumana ndi mavuto azachuma, matenda kapena mukuzunzidwa? Nanga kodi nthawi zina zimakuvutani kutumikira Yehova mosangalala? Ngati zili choncho, mungalimbikitsidwe ndi chitsanzo cha Nowa, Danieli ndi Yobu. Nawonso sanali angwiro ndipo ankakumana ndi mavuto ngati amene ife timakumana nawo. Mavuto awo ena anali oopsa moti miyoyo yawo inali pa ngozi. Koma sanasiye kukhala okhulupirika komanso omvera ndipo Mulungu amaona kuti anapereka chitsanzo chabwino. (Ezek. 14:12-14) Ezekieli analemba mawu amulemba lateroli ali ku Babeloniya mu 612 B.C.E. (Ezek. 1:1; 8:1) Pa nthawiyi n’kuti mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa, ndipo unawonongedwadi mu 607 B.C.E. Panali anthu ochepa kwambiri amene anali atalembedwa chizindikiro kuti adzapulumuka chifukwa choti anali ndi makhalidwe abwino ngati a Nowa, Danieli ndi Yobu. (Ezek. 9:1-5) Ena mwa anthuwo anali Yeremiya, Baruki, Ebedi-meleki ndiponso Arekabu. Masiku anonso, anthu amene Yehova amawaona kuti ali ndi makhalidwe abwino ngati a Nowa, Danieli ndi Yobu ndi amene adzalembedwe chizindikiro choti adzapulumuka dziko loipali likamadzawonongedwa.—Chiv. 7:9, 14. w18.02 3-4 ¶1-3
Loweruka, May 4
Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.—Mlal. 12:1.
Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimangochita zinthu zauzimu chifukwa choti n’zimene makolo anga amafuna kuti ndizichita? Kodi ineyo pandekha ndikuyesetsa kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu?’ Koma kunena zoona, si achinyamata okha amene ayenera kukhala ndi zolinga zauzimu. Zili choncho chifukwa zolinga zauzimu zimathandiza mtumiki wa Yehova aliyense kuti akhale wolimba mwauzimu. (Mlal. 12:13) Tikazindikira zinthu zina zimene sitichita bwino tiyenera kuyesetsa kuti tisinthe. Kukhala munthu wauzimu n’kofunika kwambiri chifukwa kupanda kutero sitingadzapulumuke. (Aroma 8:6-8) Yehova sayembekezera kuti tizichita zinthu popanda kulakwitsa chilichonse ndipo amatipatsa mzimu wake woyera kuti uzitithandiza. Komabe ifeyo patokha tiyenera kuchita khama. N’zoona kuti kuwerenga Baibulo n’kosangalatsa koma ndi losiyana ndi mabuku amene timawerenga pongofuna kusangalala. Tikamawerenga Baibulo, tiyenera kuchita khama kuti tipeze mfundo zamtengo wapatali zimene zingatithandize. w18.02 25 ¶10-11
Lamlungu, May 5
Nanga ukuchedweranji? Nyamuka, ubatizidwe.—Mac. 22:16.
Sikuti munthu amafunika kudziwa zinthu zambirimbiri kuti ayenerere kudzipereka komanso kubatizidwa. Paja Mkhristu aliyense akabatizidwa amafunika kupitiriza kuphunzira kuti adziwe Malemba molondola. (Akol. 1:9, 10) Ndiye kodi munthu amafunika kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti abatizidwe? Zimene zinachitikira banja lina m’mbuyomu zingatithandize kuyankha funso limeneli. (Mac. 16:25-33) Paulo ali pa ulendo wachiwiri waumishonale cha mu 50 C.E., anafika ku Filipi. Iye anali ndi Sila ndipo ali kumeneko ananamiziridwa mlandu n’kumangidwa. Ndiyeno usiku kunachitika chivomezi chomwe chinagwedeza ndendeyo n’kutsegula zitseko zake. Woyang’anira ndendeyo ankafuna kudzipha poganiza kuti akaidi onse athawa, koma Paulo anamuletsa. Kenako Paulo ndi Sila analalikira woyang’anira ndendeyo ndi banja lake. Kodi banjalo linatani litakhulupirira mfundo zokhudza Yesu zimene linaphunzira pa nthawiyo? Iwo anabatizidwa nthawi yomweyo. w18.03 10 ¶7-8
Lolemba, May 6
Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.—Sal. 144:15.
Yehova ndi Mulungu wachimwemwe ndipo amafuna kuti anthu ake azikhalanso osangalala. Mosiyana ndi anthu odzikonda amene amangofuna kuti zinthu ziziwayendera iwowo basi, atumiki a Yehova amasangalala akamadzipereka pothandiza anthu ena. (Mac. 20:35; 2 Tim. 3:2) Kodi tingadziwe bwanji ngati tayamba kudzikonda kwambiri kuposa Mulungu? Taganizirani malangizo amene akupezeka palemba la Afilipi 2:3, 4. Lembali limati: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimatsatira malangizo amenewa? Kodi ndimayesetsa ndi mtima wonse kuchita zimene Mulungu amafuna? Nanga kodi ndimayesetsa kuthandiza anthu ena mumpingo komanso mu utumiki?’ Kuchita zimenezi si kophweka chifukwa pamafunika khama komanso kudzimana zinthu zina. Komatu palibe zimene zingatithandize kukhala osangalala kuposa kudziwa kuti tikusangalatsa Wolamulira chilengedwe chonse. w18.01 23-24 ¶6-7
Lachiwiri, May 7
Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro.—2 Akor. 13:5.
Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera ‘kudziyesa kuti tione ngati tidakali olimba m’chikhulupiriro.’ Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti ndili m’gulu lokhalo limene Yehova akuligwiritsa ntchito kuti akwaniritse cholinga chake? Kodi ndikuchita zonse zimene ndingathe polalikira ndiponso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu? Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti tili m’masiku otsiriza ndipo ulamuliro wa Satana watsala pang’ono kuwonongedwa? Kodi ndimakhulupirira kwambiri Yehova ndi Yesu ngati mmene ndinkachitira pamene ndinadzipereka kwa Yehova Mulungu?’ (Mat. 24:14; 2 Tim. 3:1; Aheb. 3:14) Kuganizira mafunso oterewa kungatithandize kudziyesa kuti tidziwe kuti ndife otani.Tiyenera kuwerenga ndiponso kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo zimene zimafotokoza kufunika kwa Chikumbutso. (Yoh. 3:16; 17:3) Popanda ‘kuphunzira ndi kudziwa’ Yehova komanso kukhulupirira Mwana wake Yesu, sitingadzapeze moyo wosatha. Choncho pokonzekera Chikumbutso, mungachite bwino kuphunzira nkhani zimene zingakuthandizeni kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu. w18.01 13 ¶5-6
Lachitatu, May 8
Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.—Yoh. 6:44.
Tikamawerenga Baibulo kapena mabuku athu komanso kupezeka pamisonkhano, timamva mmene Yehova anathandizira anthu ena kuti akhalebe okhulupirika. Koma pamene mukukula mwauzimu mumafunika kuona nokha Yehova akukuthandizani. Nanga inuyo Yehova wakuthandizani m’njira ziti? Njira imodzi imene Yehova wasonyezera ubwino wake kwa Mkhristu aliyense ndi yomuthandiza kuti amuyandikire iyeyo komanso Mwana wake. Mwina wachinyamata angaganize kuti, ‘Yehova anakoka makolo anga ndipo ine ndimangowatsatira.’ Koma ngati munadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa, munasonyeza kuti inuyo muli pa ubwenzi wapadera ndi Yehovayo moti amakudziwani bwino. Pa nkhani imeneyi, Baibulo limati: “Ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziwika kwa Mulungu.” (1 Akor. 8:3) Choncho muziyamikira kwambiri mwayi umene muli nawo wokhala m’gulu la Yehova. w17.12 26 ¶12-13
Lachinayi, May 9
Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.—Aheb. 12:6.
Mawu amene anamasuliridwa kuti “chilango” m’malemba ena, angamasuliridwenso kuti “malangizo.” Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito limodzi ndi mawu ngati kudziwa zinthu, nzeru, chikondi kapena moyo. (Miy. 1:2-7; 4:11-13) Mulungu amatipatsa chilango kapena malangizo chifukwa chotikonda komanso n’cholinga choti tidzapeze moyo wosatha. (Aheb. 12:6) Ngakhale kuti amatipatsa chilango, sachita zimenezi mwankhanza. Mawu amene anamasuliridwa kuti chilango kapena malangizo nthawi zambiri amanena za kuphunzitsa munthu, ngati mmene makolo amaphunzitsira mwana amene amamukonda. Akhristufe tili ngati ana a m’nyumba ya Mulungu. (1 Tim. 3:15) Choncho timazindikira kuti Yehova ali ndi ufulu wotipatsa malamulo komanso chilango tikapanda kumvera malamulowo. Ndipotu tikakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zathu, chilango chake chingatithandize kwambiri kuzindikira kufunika komumvera.—Agal. 6:7. w18.03 23 ¶1; 24 ¶3
Lachisanu, May 10
Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu, ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.—Miy. 17:27.
Ngati ndinu wachinyamata ndipo mumaona kuti makolo anu sakumvetsani komanso amakupanikizani, kodi mungatani? Maganizo amenewa akhoza kukuchititsani kuganiza kuti si nzeru kutumikira Yehova ndipo ngati maganizo amenewa atakula mukhoza kusiyadi kumutumikira. Koma dziwani kuti mukasiya, mudzaona nokha kuti palibenso anthu ena amene amakukondani ndi mtima wonse ngati mmene amachitira makolo anu komanso abale ndi alongo. Ndipo ngati makolo anu sakulangizani, zingakhale zokayikitsa kuti amakukondani ndi mtima wonse. (Aheb. 12:8) Mwina njira imene makolowo amakulangizirani ndi imene sikusangalatsani. Koma m’malo mongoipidwa ndi mmene amaperekera malangizo, muyenera kuganizira chimene chimawapangitsa kuchita zimenezo. Choncho muyenera kukhala odekha ndipo muziyesetsa kuti musamakwiye msanga akamakudzudzulani. Yesetsani kuchita zinthu ngati wozindikira ndipo mukamalangizidwa muzimvetsera mofatsa. Muziyesetsa kuona mmene mungagwiritsire ntchito malangizowo popanda kuganizira kwambiri mmene akuwaperekera.—Miy. 1:8. w17.11 29 ¶16-17
Loweruka, May 11
Wasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.—Chiv. 2:4.
Mwina mwaona achinyamata ena amene anabatizidwa koma pakapita nthawi anayamba kukayikira ngati ndi nzeru kutsatira mfundo za m’Baibulo. Ana ena amafika posiya kutumikira Yehova. Ndiye mwina mumaganiza kuti mwana wanu akhoza kuyamba bwinobwino kutumikira Yehova koma kenako n’kusiya. Kodi inuyo mungatani kuti mwana wanu asachite zimenezi koma apeze ‘nzeru zomuthandiza kuti adzapulumuke’? (1 Pet. 2:2) Tingapeze yankho la funsoli pa zimene Paulo analembera Timoteyo m’kalata yake. Anati: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo, chifukwa ukudziwa anthu amene anakuphunzitsa. Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.” (2 Tim. 3:14, 15) N’zochititsa chidwi kuti Paulo anatchula (1) kudziwa malemba oyera, (2) kukhulupirira pambuyo pokhutira ndi zimene waphunzira komanso (3) kupeza nzeru zothandiza kuti apulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu. w17.12 18-19 ¶2-3
Lamlungu, May 12
Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima, koma inuyo mudzalira chifukwa chopwetekedwa mtima.—Yes. 65:14.
Anthu ambiri sakhulupirira Mulungu chifukwa choti zipembedzo zambiri zimalakwitsa pophunzitsa kuti Mulungu amaotcha anthu, pokakamiza anthu kuti azipereka ndalama komanso polimbikitsa zandale. M’pake kuti anthu ambiri amaona kuti akhoza kukhala osangalala popanda kukhala m’chipembedzo chilichonse. N’zoona kuti munthu akhoza kukhala wosangalala popanda kukhala m’chipembedzo chonyenga, koma n’zosatheka kukhala wosangalala ngati sali pa ubwenzi ndi Yehova yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Chilichonse chimene Mulungu amachita chimakhala chothandiza kwa ena. Atumiki ake amasangalalanso chifukwa choti amakonda kuthandiza anzawo. (Mac. 20:35) Mwachitsanzo, taganizirani mmene chipembedzo choona chimathandizira mabanja kuti akhale osangalala. Paja chimaphunzitsa anthu okwatirana kuti azilemekezana, aziona kuti ukwati ndi wopatulika, azipewa chigololo, aziphunzitsa ana awo kuti akhale aulemu komanso kuti azikonda anzawo ndi mtima wonse. Zonsezi zimathandiza kuti atumiki a Yehova azikhala osangalala ndiponso ogwirizana m’mipingo yawo komanso padziko lonse. w17.11 21-22 ¶6-7
Lolemba, May 13
Munthu wovutika ine!—Aroma 7:24.
Pali atumiki a Yehova ambirimbiri amene adandaulapo chonchi. Tonsefe tinatengera uchimo kwa makolo athu ndipo tikachita zinthu zimene tikudziwa kuti Mulungu sangasangalale nazo timavutika kwambiri mumtima. Akhristu ena amene anachita tchimo lalikulu amaganiza kuti Mulungu sangawakhululukirenso. Koma Malemba amatitsimikizira kuti anthu amene amathawira kwa Yehova sayenera kudziimba mlandu mopitirira malire. (Sal. 34:22) Mtumwi Paulo atadandaula kuti akulephera kumvera Yehova bwinobwino, sanakayikire kuti Mulungu amukhululukira ndipo anati: “Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) N’zoona kuti Paulo ankalimbana ndi uchimo ndipo anali atalakwitsapo zinthu n’kulapa, koma sankakayikira kuti Mulungu amukhululukira kudzera mwa Yesu. Dipo la Yesu limathandiza kuti tikhale ndi chikumbumtima choyera komanso mtendere wamumtima. (Aheb. 9:13, 14) Popeza Yesu ndi Mkulu wa Ansembe, “akhoza kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.”—Aheb. 7:24, 25. w17.11 8 ¶1-2; 12 ¶15
Lachiwiri, May 14
Lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.—Sal. 76:11.
Kodi tingakwaniritse bwanji lumbiro limeneli? Zimene timachita tikakumana ndi mayesero, kaya aakulu kapena aang’ono, ziyenera kusonyeza kuti timafunitsitsa kukwaniritsa lonjezo loti tizitamanda Yehova “tsiku ndi tsiku.” (Sal. 61:8) Mwachitsanzo, kodi tingatani ngati munthu wina kuntchito kapena kusukulu akutikopa? Kodi tidzakana zimene akufunazo n’cholinga choti tisonyeze kuti ‘timasangalala ndi njira’ za Yehova? (Miy. 23:26) Ngati anthu ena m’banja lathu si Mboni, kodi timapempha Yehova kuti atithandize kukhalabe ndi khalidwe labwino ngakhale pamene anthu enawo sakuchita zimenezo? Kodi tsiku lililonse timapemphera kwa Yehova n’kumamuthokoza chifukwa choti amatikonda komanso kutilamulira bwino? Kodi timayesetsa kuwerenga Baibulo tsiku lililonse? Pajatu tinalonjeza kuti tizichita zinthu ngati zimenezi. Tikamamvera Yehova ndiponso kumulambira ndi mtima wonse timasonyeza kuti timamukonda komanso tinadziperekadi kwa iye. Tiyenera kuona kuti kulambira Mulungu n’kofunika kwambiri pa moyo wathu, osati kumangomulambira mwamwambo chabe. w17.10 23-24 ¶11-12
Lachitatu, May 15
Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.—Sal. 147:1.
Munthu wina wotchuka amene amapeka nyimbo ananena kuti mawu ongolankhulidwa komanso nyimbo zoimbidwa ndi zida zokha zikhoza kufika munthu pamtima. Koma nyimbo zokhala ndi mawu ndi zimene zimafika kwambiri munthu pamtima. Palibe mawu a m’nyimbo amene tingafune kuti atifike pamtima kuposa mawu amene ali m’nyimbo zotamanda Atate wathu wakumwamba. M’pake kuti kuimba nyimbo patokha kapena ndi mpingo n’kofunika kwambiri polambira Yehova. Koma kodi inuyo mumakonda kuimba mokweza mumpingo, kapena mumachita manyazi? M’zikhalidwe zina, amuna sakonda kuimba pa gulu. Koma ngati anthu amene akutsogolera mumpingo saimba mokweza kapena ngati amatanganidwa ndi zinthu zina pamene nyimbo zikuimbidwa, zimasokoneza mpingo wonse. (Sal. 30:12) Ngati timaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri polambira Yehova, tiyenera kuyesetsa kupezeka pa nthawi imene nyimbo zikuimbidwa ndipo tisamatuluke. w17.11 3 ¶1-3
Lachinayi, May 16
Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere koma lupanga.—Mat. 10:34.
Tonse timafuna kukhala moyo wamtendere, wopanda nkhawa. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa amatipatsa “mtendere wa Mulungu,” umene ndi mtendere wamumtima womwe umatithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri. (Afil. 4:6, 7) Tikadzipereka kwa Yehova, timakhalanso pa “mtendere ndi Mulungu,” zomwe zikutanthauza kuti timakhala naye pa ubwenzi. (Aroma 5:1) Komabe nthawi ya Mulungu yoti tikhale pa mtendere ndi anthu onse sinafike. M’masiku otsirizawa, kukuchitika mikangano yambiri ndipo anthu ambiri ali ndi mtima wokonda kuyambana ndi anzawo. (2 Tim. 3:1-4) Akhristufe tiyenera kumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndiponso mfundo zabodza zimene amaphunzitsa. (2 Akor. 10:4, 5) Koma nthawi zambiri mtendere wathu umasokonekera chifukwa cha achibale athu omwe si Mboni. Ena angamanyoze mfundo zimene timakhulupirira, kutinena kuti tikugawanitsa banja lathu kapena angamatiopseze kuti tikapitiriza sazitionanso ngati achibale awo. w17.10 12 ¶1-2
Lachisanu, May 17
Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.—Sal. 119:97.
Zilankhulo zimene Baibulo linamasuliridwa zimasintha pakapita nthawi. Choncho Baibulo limene poyamba linkathandiza kwambiri anthu pakapita nthawi limakhala losathandiza chifukwa cha kusintha kwa chilankhulo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Baibulo lina limene linamasuliridwa m’Chingelezi. Baibulo lake ndi la King James Version lomwe linatuluka mu 1611. Anthu ambiri ankakonda Baibuloli ndipo mawu ake ena okuluwika anayamba kugwiritsidwa ntchito kwambiri m’Chingelezi. Koma patapita nthawi, mawu ambiri a m’Baibulo limeneli anayamba kumveka achikale. Umu ndi mmenenso zilili ndi Mabaibulo amene anamasuliridwa m’zilankhulo zina. N’chifukwa chake tikuyamikira kwambiri kuti tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomasuliridwa m’chilankhulo chamakono. Baibulo limeneli likupezeka lonse kapena mbali zake m’zilankhulo zoposa 150. Choncho anthu ambiri padziko lonse akhoza kulipeza. Popeza kuti mawu ake ndi osavuta kumva, uthenga wake umafika anthu pamtima. w17.09 19 ¶5-6
Loweruka, May 18
Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.—Miy. 27:11.
Achinyamata amafunika kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Iwo amafunika kulimba mtima kuti asankhe bwino pa nkhani monga anthu ocheza nawo, zosangalatsa, kupewa makhalidwe oipa komanso kuti abatizidwe. Tikutero chifukwa choti Satana, yemwe amatonza Mulungu, safuna kuti achinyamata asankhe bwino pa nkhani zimenezi. Achinyamata amafunika kusankha zoti achite pa moyo wawo ndipo nkhani imeneyi ndi yofunika kwambiri. M’mayiko ena, achinyamata amalimbikitsidwa kuti aphunzire kwambiri kuti adzapeze ntchito yapamwamba. Ndipo m’mayiko ena, mavuto azachuma amachititsa achinyamata kuona kuti ayenera kuyesetsa kupeza ndalama zothandizira achibale awo. Achinyamata amene amalimba mtima n’kusankha kuti aziika kutumikira Yehova pamalo oyamba adzadalitsidwa kwambiri. Iye adzawathandiza kupeza zofunika pa moyo wawo komanso wa achibale awo. Munthawi ya atumwi, wachinyamata wina dzina lake Timoteyo anasankha kuchita zimenezi ndipo umenewu ndi umboni wakuti nanunso mukhoza kukwanitsa.—Afil. 2:19-22. w17.09 29-30 ¶10-12
Lamlungu, May 19
Buku la malamulo ili lisachoke pakamwa pako . . . uonetsetse kuti ukutsatira zonse zolembedwamo. Pakuti ukatero, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzachita zinthu mwanzeru.—Yos. 1:8.
Kuphunzira Baibulo mwakhama nthawi zonse kungatithandize kuti tikhale odziletsa. Zili choncho chifukwa chakuti m’Baibulo muli nkhani zosonyeza ubwino wa kudziletsa komanso mavuto amene angabwere chifukwa cholephera kuchita zimenezi. Yehova anakonza zoti nkhani zimenezi zilembedwe m’Baibulo n’cholinga choti zitithandize. (Aroma 15:4) Choncho ndi bwino kuziwerenga, kuziganizira kwambiri ndiponso kuona zimene tikuphunzirapo. Tiziganizira mmene zingatithandizire ifeyo komanso banja lathu. Tizipemphanso Yehova kuti atithandize kutsatira Mawu ake. Muzivomerezanso ngati muli ndi vuto linalake pa nkhani yodziletsayi. Ndiyeno muziipempherera nkhaniyo ndiponso kuona zimene mungachite kuti musinthe. (Yak. 1:5) Mungachite bwino kufufuza nkhani zimene gulu lathu lafalitsa zomwe zingakuthandizeni kuthana ndi vuto lililonse limene muli nalo. w17.09 6 ¶15-16
Lolemba, May 20
Muvale umunthu watsopano.—Akol. 3:10.
“Umunthu watsopano” “unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu” ndipo n’zotheka kukhala nawo. (Aef. 4:24) Tikutero chifukwa chakuti Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake choncho n’zotheka kusonyeza makhalidwe ake abwino. (Gen. 1:26, 27; Aef. 5:1) Paulo atanena kuti tiyenera kuvala umunthu watsopano, anafotokoza kufunika kokhala opanda tsankho. Khalidweli ndi mbali ina yofunika ya umunthu watsopano. Iye anati: “Sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu.” N’chifukwa chiyani Akhristufe sitiyenera kusankha anthu chifukwa cha mtundu wawo, dziko lawo kapena chuma chawo? Zili choncho chifukwa Baibulo limanena kuti tili ngati “munthu mmodzi,” kutanthauza kuti ndife ofanana. (Akol. 3:11; Agal. 3:28) Akhristu amene avala umunthu watsopano amalemekeza Akhristu anzawo komanso anthu ena mosaganizira mtundu wawo kapena chikhalidwe chawo.—Aroma 2:11. w17.08 22 ¶1; 23 ¶3-4
Lachiwiri, May 21
Yehova azidzayembekezera.—Yes. 30:18.
Sikuti Yehova amangotiuza kuti tiziyembekezera moleza mtima koma nayenso amaleza mtima. Iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. (2 Pet. 3:9) Mwachitsanzo, zaka masauzande m’mbuyomo, Satana ananena kuti Yehova salamulira bwino. Komabe Yehova wakhala akuyembekezera moleza mtima nthawi yoti athetse nkhaniyi n’kuyeretsa dzina lake. Zimenezi zidzathandiza kuti anthu amene “amamuyembekezera” adzalandire madalitso osaneneka. (Yes. 30:18) Nayenso Yesu amatha kudikira moleza mtima. Pamene anali padzikoli anasonyeza kuti ndi wokhulupirika ndipo anapereka nsembe ya dipo mu 33 C.E., koma anadikira mpaka mu 1914 kuti ayambe kulamulira. (Mac. 2:33-35; Aheb. 10:12, 13) Ndipo adzadikirabe mpaka pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 kuti adani ake onse atheretu. (1 Akor. 15:25) Koma kudikira kwakeko sikudzapita pachabe. w17.08 7 ¶16-17
Lachitatu, May 22
Mulungu amene . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.—2 Akor. 1:3, 4.
Mlongo wina dzina lake Susi ananena kuti: “Mwana wathu atamwalira, zinatipweteka koopsa pafupifupi kwa chaka chathunthu.” Nayenso m’bale wina ananena kuti mkazi wake atamwalira mwadzidzidzi, ankamva “ululu winawake wosaneneka.” Koma chomvetsa chisoni ndi chakuti mavuto ngati amenewa akuchitikira anthu ambiri. Ndipo Akhristu ambiri sankayembekezera kuti anthu amene amawakonda akhoza kumwalira Aramagedo isanachitike. Kaya nafenso tinaferedwa kapena ayi, tikhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu oferedwa angalimbikitsidwe bwanji?’ Mwina munamva anthu akunena kuti nthawi ikamapita chisoni chimatha. Koma kodi ndi zoona kuti munthu amasiyadi kumva chisoni pakangopita nthawi? Mlongo wina wamasiye ananena kuti: “Ine ndimaona kuti zimene munthu amachita nthawi ikamadutsa n’zimene zimathandiza kuti ayambe kumva bwino.” Mofanana ndi bala kapena chilonda, chisoni chimatha mumtima mwa munthu ngati munthuyo akusamalira mtima wakewo. w17.07 12-13 ¶1-3
Lachinayi, May 23
Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.—Sal. 37:4.
Kodi Yehova amafuna kuti zolinga zanu zikhale zotani? Iye analenga anthu m’njira yoti azisangalala akamamudziwa bwino komanso kumutumikira mokhulupirika. (Sal. 128:1; Mat. 5:3) Anthufe ndi osiyana kwambiri ndi nyama. Tikutero chifukwa chakuti pa moyo wa nyama, chofunika ndi kudya, kumwa ndi kuswana basi. Koma Mulungu amafuna kuti anthufe tizikhala ndi zolinga zinanso zomwe zingatithandize kukhala osangalala. Mlengi wathu ndi “Mulungu wachikondi” komanso “Mulungu wachimwemwe” ndipo anatilenga “m’chifaniziro chake.” (2 Akor. 13:11; 1 Tim. 1:11; Gen. 1:27) Tikamatsanzira Mulungu wathu wachikondi timasangalala. Paja Baibulo limati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Mfundo imeneyi ndi yoona ndipo mwina inuyo mwatsimikizapo zimenezi. Choncho Yehova amafuna kuti zolinga zathu zizisonyeza kuti timakonda Mulungu komanso anthu ena.—Mat. 22:36-39. w17.07 23 ¶3
Lachisanu, May 24
Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.—Sal. 84:11.
Mulungu amalemekeza kwambiri atumiki ake apadzikoli. Amatisamaliranso kuposa mmene tingadzisamalire tokha. Sikuti Yehova amangosamalira anthu ake monga gulu koma amaganiziranso munthu aliyense payekha. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Yehova anachita kwa zaka 300 pamene ankagwiritsa ntchito oweruza populumutsa Aisiraeli kwa adani awo. Pa nthawi yovutayi, iye ankaganiziranso munthu aliyense payekha. Anaona zimene munthu wina dzina lake Rute anachita. Iye anasiya anthu a mtundu wake n’kuyamba kulambira Yehova limodzi ndi Aisiraeli. Yehova anadalitsa Rute pomupatsa mwamuna wabwino komanso mwana wamwamuna. Komatu si zokhazi. Rute akadzaukitsidwa adzamva kuti mwana wake anali mumzere wa makolo a Mesiya. Adzasangalalanso kuzindikira kuti nkhani yake inalembedwa m’buku la m’Baibulo lodziwika ndi dzina lake.—Rute 4:13; Mat. 1:5, 16. w17.06 28-29 ¶8-9
Loweruka, May 25
Mzimu woyera . . . [adzakukumbutsani] zonse zimene ndinakuuzani.—Yoh. 14:26.
Mu 1970, m’bale wina dzina lake Peter anali atangoyamba kumene kutumikira pa Beteli ku Britain ndipo n’kuti ali ndi zaka 19. Tsiku lina akulalikira kunyumba ndi nyumba anakumana ndi bambo winawake wandevu zake. Peter anafunsa bamboyo ngati akufuna kudziwa bwino Baibulo. Popeza bamboyo ankadziona kuti amadziwa Baibulo, anadabwa n’kunena kuti onse m’nyumbayo ndi arabi achiyuda. Pofuna kumuyesa, bamboyo anafunsa kuti: “Mnyamata iwe, kodi buku la Danieli linalembedwa m’chilankhulo chanji?” Peter anayankha kuti: “Mbali ina inalembedwa m’Chiaramu.” Iye atafotokoza zimenezi, rabiyo anadabwa kuti Peter akudziwa yankho la funsolo. Nayenso Peter anadabwa kwambiri kuti wadziwa bwanji yankholo. Atafika kunyumba anafufuza m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amene anawerenga ndipo anapeza nkhani yofotokoza kuti mbali ina ya buku la Danieli inalembedwa m’Chiaramu. (Dan. 2:4) Izi zikusonyezeratu kuti mzimu woyera ungatithandize kukumbukira zinthu zimene tinawerenga kale.—Luka 12:11, 12; 21:13-15. w17.06 13 ¶17
Lamlungu, May 26
Olowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.—1 Akor. 7:28.
Banja likhoza kukumana ndi mavuto ena mkazi akakhala woyembekezera. N’zoona kuti banja limasangalala likadziwa kuti lidzakhala ndi mwana. Komabe likhoza kuda nkhawa poganiza kuti, ‘Kodi mayiyo adzabereka bwinobwino, nanga mwanayo adzabadwa wathanzi?’ Banjalo limaderanso nkhawa mavuto azachuma amene angakumane nawo akakhala ndi mwana. Ndipotu mwanayo akabadwa mavuto enanso akhoza kuyamba. Zili choncho chifukwa chakuti nthawi imene mayi amakhala akusamalira mwana imakhala yambiri ndipo izi zingachititse kuti mwamuna aziona ngati akunyalanyazidwa. Komanso udindo wa mwamunayo umawonjezereka chifukwa amafunika kusamaliranso mwanayo ndiponso kumupezera zofunika pa moyo. Koma mabanja ena amakhala ndi vuto lina. Iwo amafunitsitsa kukhala ndi mwana koma sizitheka. Mkazi akhoza kudandaula kwambiri chifukwa choti sakubereka. w17.06 4 ¶1; 5 ¶5-6
Lolemba, May 27
Mawu anu amatsekemera m’kamwa mwanga, Kuposa mmene uchi umakomera!—Sal. 119:103.
Akhristufe timakonda kwambiri choonadi ndipo timadziwa kuti chimapezeka m’Mawu a Mulungu. Paja popemphera kwa Atate wake, Yesu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yoh. 17:17) Choncho kuti munthu akonde choonadi, ayenera kudziwa kaye Mawu a Mulungu. (Akol. 1:10) Komabe kungodziwa Mawuwo si kokwanira. Munthu yemwe analemba Salimo 119 anatithandiza kumvetsa tanthauzo la kukonda choonadi. (Sal. 119:97-100) Tsiku lililonse tiyenera kupeza mpata woganizira kwambiri zimene tawerenga m’Baibulo. Tikhoza kukonda kwambiri choonadi tikamaganiziranso mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira. Mfundo zimene timaphunzira m’gulu la Mulunguzi zingakhale zokoma ngati uchi. Tikamaziganizira kwambiri zingakhale ngati tikumva kutsekemera kwa “mawu okoma” m’kamwa mwathu. Ndipo izi zingathandize kuti tizikumbukira mfundozo komanso kuzigwiritsa ntchito.—Mlal. 12:10. w17.05 19-20 ¶11-12
Lachiwiri, May 28
Zoonadi Mulungu ali pakati panu.—1 Akor. 14:25.
Tiyenera kuthandiza anthu ovutika ngakhale omwe si Mboni. (Luka 10:33-37) Njira yabwino yowathandizira ndi yowauza uthenga wabwino. Mkulu wina amene anathandiza anthu ambiri othawa kwawo anati: “Tiyenera kuyamba n’kuwadziwitsa kuti ndife a Mboni za Yehova ndipo cholinga chathu chachikulu n’kuwathandiza kuti aphunzire za Yehova osati kuwapezera zinthu. Kupanda kutero angayambe kucheza nafe n’cholinga choti angopeza kenakake.” Tikamasonyeza chikondi kwa alendo, zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri. (Sal. 146:9) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Eritrea dzina lake Alganesh. Mwamuna wake anamwalira ndipo iye ataona kuti anthu akuzunzidwa kwambiri anathawa m’dzikoli ndi ana ake 6. Anayenda ulendo wodutsa m’chipululu kwa masiku 8 kenako anakafika ku Sudan. Iye anati: “Abale a m’dzikoli anatilandira ngati kuti ndife achibale awo enieni. Anatipatsa chakudya, zovala, malo ogona komanso ankatithandiza pa nkhani ya mayendedwe. A Mboni za Yehova okha ndi amene amalandira anthu achilendo kunyumba zawo chifukwa choti amalambira Mulungu mmodzi.”—Yoh. 13:35. w17.05 7 ¶17, 19-20
Lachitatu, May 29
Simunanene zoona za ine monga wachitira Yobu mtumiki wanga.—Yobu 42:8.
“Kodi mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu? Kodi aliyense wozindikira angakhale waphindu kwa iye? Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama?” (Yobu 22:1-3) Elifazi wa ku Temani ndi amene anafunsa Yobu mafunso amenewa. Kodi inuyo mukuganiza kuti yankho la mafunsowa ndi chiyani? Elifazi ankaganiza kuti yankho la mafunso amenewa ndi lakuti ayi. Komanso Bilidadi wa ku Shuwa ananena kuti n’zosatheka kuti Yehova aone kuti munthu ndi wolungama. (Yobu 25:4) Elifazi ndi Bilidadi ankafuna kuti Yobu aziona ngati Yehova sankayamikira zabwino zimene ankachita pomutumikira. Iwo ankafuna kuti Yobu aziganiza zoti Yehova ankaona kuti iye ndi wonyozeka ngati kadziwotche, mphutsi kapena nyongolotsi. (Yobu 4:19; 25:6) Yehova anadzudzula Elifazi, Bilidadi ndi Zofari chifukwa chonama kuti iye sankasangalala ndi Yobu ndipo anatchula Yobuyo kuti “mtumiki wanga.” (Yobu 42:7) Izi zikusonyeza kuti munthu ndi “waphindu kwa Mulungu.” w17.04 28 ¶1-2
Lachinayi, May 30
Adzasangalala ndi mtendere wochuluka.—Sal. 37:11.
Anthufe takhala m’dziko loipali kwa nthawi yaitali moti mavuto tangofika powazolowera. Tili ngati anthu amene amakhala pafupi ndi siteshoni ya sitima moti angozolowera phokoso lake kapena anthu amene amakhala pafupi ndi kumtaya moti angozolowera fungo loipa. Anthu amene amakhala pamalo otere amazindikira kuti anali pa mavuto, pa nthawi imene vutolo latha. N’chiyani chidzalowe m’malo mwa nkhawa zimene timakhala nazo masiku ano? Taganizirani lonjezo lamulemba la lero. Kodi inuyo mumamva bwanji mukawerenga mawu amenewa? Zimenezitu n’zimene Yehova adzatichitire. Choncho tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti tisachoke m’gululi komanso kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova m’masiku ovutawa. Muziganizira kwambiri zimene Yehova watilonjeza ndipo musamakayikire kuti zidzachitika. Muziuzanso anthu ena zinthu zimenezi. (1 Tim. 4:15, 16; 1 Pet. 3:15) Mukamatero, simudzapita dziko loipali likamadzapita. Koma mudzakhala ndi moyo wosangalala mpaka kalekale. w17.04 13 ¶16-17
Lachisanu, May 31
Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.—Yak. 3:2.
Timadziwa bwino kuti tonsefe timalakwitsa zinthu zina. Koma kodi timatani m’bale wina akatilakwira? Kodi mudzaona zinthu mmene Mulungu amazionera? Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mkulu walankhula mawu osonyeza tsankho? Nanga mungatani ngati mkulu walankhula mawu amene akukhumudwitsani kapena kukupwetekani kwambiri? Kodi mungathamangire kuganiza kuti sakuyeneranso kukhala mkulu? Kapena kodi mungasiye nkhaniyo m’manja mwa Yesu yemwe ndi mutu wa mpingo? M’malo moganizira kwambiri zinthu zimene m’baleyo walakwitsa, ndi bwino kuganizira zaka zambirimbiri zimene watumikira mokhulupirika. Ngati m’bale amene wakulakwiraniyo akutumikirabe monga mkulu kapena wapatsidwa udindo wina, kodi mungasangalale naye limodzi? Mukakhululuka mumasonyeza kuti mukutsanzira Yehova pa nkhani ya chilungamo.—Mat. 6:14, 15. w17.04 27 ¶18