April
Lolemba, April 1
Anapereka mphatso za amuna.—Aef. 4:8.
Kodi tingatani kuti mphatso zimenezi zizitithandiza? Choyamba, tiyenera kutsanzira chikhulupiriro komanso chitsanzo chabwino cha akuluwo. Njira ina ndi kutsatira malangizo amene amatipatsa. (Aheb. 13:7, 17) Tizikumbukira kuti akulu amatikonda ndipo amafuna kuti tizikula mwauzimu. Mwachitsanzo, akaona kuti tayamba kuphonya misonkhano kapena sitikuchitanso zinthu mwakhama amatithandiza mwamsanga. Iwo amamvetsera mavuto athu, kutilimbikitsa ndi malemba oyenerera komanso kutipatsa malangizo othandiza. Kodi inuyo mumaona kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova amakukondani? Tisaiwale kuti sizikhala zophweka kuti akulu abwere kudzatipatsa malangizo. Ndiye kodi tingatani kuti tiziwapeputsira akulu ntchito yawo mumpingo? Tiyenera kukhala odzichepetsa, omasuka komanso oyamikira. Tiziona kuti thandizo lililonse limene angatipatse likuchokera kwa Yehova. Tikamatero zinthu zidzatiyendera bwino komanso tidzathandiza kuti akuluwo azigwira ntchito yawo mosangalala. w18.03 31-32 ¶15-16
Lachiwiri, April 2
Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.—Miy. 27:11.
Ana amakhala osiyana ndipo aliyense amaphunzira zinthu mosiyana ndi mnzake. Ana ena amayamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu ali aang’ono ndipo amafuna kubatizidwa. Koma ena sachita zimenezi mpaka atakulirapo. Choncho makolo anzeru sakakamiza ana awo kuti abatizidwe. M’malomwake amathandiza mwana aliyense kuti aphunzire zinthu mogwirizana ndi msinkhu wake komanso luso lake lomvetsa zinthu. Makolo angasangalale mwana wawo akamakumbukira mfundo ya palemba lalero. Komabe sayenera kuiwala cholinga chawo chothandiza ana awo kuti akhale Akhristu obatizidwa. Choncho makolo angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi mwana wathu akudziwa zinthu zokwanira moti angayenerere kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa?’ w18.03 9-10 ¶6
Lachitatu, April 3
Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.—Sal. 15:4.
Anthu ena akatiitana ife n’kuvomera, si bwino kungosintha popanda zifukwa zomveka. N’kutheka kuti woitanayo anachita zambiri pokonzekera ndiye zonse zimene wachita zingakhale zopanda ntchito. (Mat. 5:37) Ena amavomera akaitanidwa ndi munthu koma n’kusintha chifukwa choti aitanidwanso ndi anthu ena amene akuganiza kuti akhoza kusangalala nawo kwambiri. Kodi zimenezi zingasonyeze kuti ndife achikondi komanso aulemu? Ndiyetu tikaitanidwa n’kuvomera tiyenera kuyamikira zilizonse zimene oitanawo angatipatse. (Luka 10:7) Koma ngati pali zifukwa zomveka zimene zingatilepheretse, tiyenera kudziwitsa wotiitanayo mwamsanga. Chinthu china chofunika ndi kulemekeza chikhalidwe cha amene atiitana. M’madera ena, munthu akhoza kungofika pakhomo kudzacheza koma m’madera ena pamafunika kuneneratu tisanapite kwa munthu. M’madera enanso, mlendo amafunika kukana kamodzi kapena kawiri akaitanidwa kenako amavomera pomwe kwina ukangokana, ngakhale kamodzi, zimaoneka kuti sukufuna. Ndiye chofunika n’kuyesetsa kuti tisakhumudwitse anthu amene atiitana. w18.03 18 ¶20-21
Lachinayi, April 4
Tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.—Aheb. 6:1.
Tisaiwale kuti kungodziwa Baibulo si kokwanira kuti munthu akhale wauzimu. (1 Maf. 4:29, 30; 11:4-6) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo? Ndi bwino kuyesetsa kuti tipitirize kukula mwauzimu. (Akol. 2:6, 7) Chinthu china chimene chingatithandize kwambiri n’kuphunzira buku lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’? Munthu akaphunzira buku lonseli amatha kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Ngati mwamaliza kuphunzira bukuli, mungachite bwino kuphunziranso mabuku ena amene angalimbitse chikhulupiriro chanu. (Akol. 1:23) Mungachitenso bwino kuganizira kwambiri zimene mukuphunzira n’kupempha Yehova kuti akuthandizeni kuzitsatira. Cholinga chathu pophunzira chizikhala choti tikhale ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova komanso kumvera malamulo ake. (Sal. 40:8; 119:97) Tiyeneranso kuyesetsa kukana zinthu zimene zingatibwezeretse m’mbuyo mwauzimu.—Tito 2:11, 12. w18.02 24-25 ¶7-9
Lachisanu, April 5
[Nowa] anakhala wolandira cholowa cha chilungamo, chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.—Aheb. 11:7.
Kuti titsanzire chikhulupiriro cha Nowa, Tiyenera kuphunzira kwambiri Mawu a Mulungu, kuganizira zimene timaphunzirazo komanso kuzitsatira pa moyo wathu. (1 Pet. 1:13-15) Tikamachita zimenezi chikhulupiriro ndiponso nzeru yochokera kwa Mulungu zidzatithandiza kupewa ziwembu za Satana komanso mzimu woipa wa m’dzikoli. (2 Akor. 2:11) Mzimuwu umalimbikitsa anthu kukonda chiwawa ndiponso chiwerewere. Umawalimbikitsanso kuganizira kwambiri zimene amalakalaka. (1 Yoh. 2:15, 16) Ukhozanso kuchititsa anthu amene afooka mwauzimu kuti azinyalanyaza umboni wakuti tsiku lalikulu la Mulungu layandikira. Kumbukirani kuti pamene Yesu anayerekezera masiku a Nowa ndi masiku ano ananena kwambiri za kusakhala tcheru mwauzimu osati za chiwawa ndi chiwerewere. (Mat. 24:36-39) Muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimachita pa moyo zimasonyeza kuti ndimamudziwa bwino Yehova? Nanga kodi chikhulupiriro changa chimandilimbikitsa kutsatira mfundo zachilungamo za Mulungu komanso kuziphunzitsa kwa anthu ena?’ Mayankho anu pa mafunsowa angakuthandizeni kudziwa ngati ‘mukuyendadi ndi Mulungu woona’ kapena ayi.—Gen. 6:9. w18.02 9-10 ¶8-10
Loweruka, April 6
Anthu amenewa uwapewe.—2 Tim. 3:5.
Sitingapeweretu anthu amakhalidwe oipa chifukwa timakhala moyandikana nawo, timagwira nawo ntchito kapena timapita nawo kusukulu. Koma n’zotheka kupewa kutengera maganizo komanso makhalidwe awo oipa. Zimenezi zingatheke tikamapitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova pophunzira Baibulo komanso kugwirizana kwambiri ndi anthu amene amamutumikira ndi mtima wonse. Tizithandizanso anthu ena kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Tiziyesetsa kupeza mpata wolalikira ndipo tizipempha Mulungu kuti atithandize kulankhula zinthu zoyenera pa nthawi yoyenera. Tiyenera kuuza anthu kuti ndife a Mboni za Yehova. Ndiye anthuwo akamaona makhalidwe athu abwino, adzalemekeza Mulungu osati ifeyo. Taphunzitsidwa “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.” (Tito 2:11-14) Tikamakhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu, anthu adzaona ndipo ena akhoza kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zek. 8:23. w18.01 31 ¶17-18
Lamlungu, April 7
Anthu adzakhala odzikonda.—2 Tim. 3:2.
Kodi n’kulakwa kudzikonda? Ayi. Kudzikonda moyenerera n’kothandiza. Yehova anatilenga m’njira yoti tizidzikonda. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Maliko 12:31) Choncho ngati sitidzikonda, sitingathe kukonda anzathu. Baibulo limanenanso kuti: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” (Aef. 5:28, 29) Choncho kudzikonda moyenerera si kulakwa. Kudzikonda kotchulidwa pa 2 Timoteyo 3:2 si kudzikonda moyenerera koma mopitirira malire. Anthu amene amadzikonda chonchi amadziganizira kwambiri kuposa mmene amayenera kuchitira. (Aroma 12:3) Iwo amangoganizira za iwowo nthawi zonse ndipo saganizira anthu ena. Zinthu zikalakwika amaloza chala ena m’malo movomereza kulakwa kwawo. Kunena zoona, anthu oterewa sakhala osangalala. w18.01 23 ¶4-5
Lolemba, April 8
Sonyezani kuti ndinu oyamikira.—Akol. 3:15.
Munthu akamaphunzira Baibulo amamvetsera mawu a Yehova koma akamapemphera amalankhula naye. Mkhristu sayenera kuganiza kuti kupemphera ndi mwambo chabe kapena chithumwa chothandiza kuti zinthu zinazake zitiyendere bwino. M’malomwake ayenera kuona kuti ndi njira imene imatithandiza kuti tilankhule ndi Mlengi wathu. Yehova amafuna kumva maganizo athu. (Afil. 4:6) Ndipo Baibulo limatilangiza kuti ngati pali zinthu zina zimene zikutisowetsa mtendere, ‘tizitulira Yehova nkhawa zathu.’ (Sal. 55:22) Kodi inuyo mumaona kuti malangizo amenewa ndi othandiza? Abale ndi alongo mamiliyoni ambiri amavomereza kuti zimenezi zimathandiza. Choncho zikhoza kukuthandizaninso inuyo. Koma si bwino kumangopemphera tikafuna kuti Yehova atithandize pa vuto linalake. Nthawi zina tikhoza kumangoganizira mavuto athu n’kuiwaliratu madalitso ambirimbiri amene tili nawo. Choncho zingakhale bwino kuti tsiku lililonse tiziganizira zinthu zabwino, mwina zokwana zitatu, zimene tiyenera kuyamikira. Kenako tizipemphera kwa Yehova n’kumuyamikira pa zinthu zimenezo. w17.12 25-26 ¶10-11
Lachiwiri, April 9
Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke.—2 Tim. 3:15.
Anthu ambiri amene amaphunzira Baibulo amadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. Ambiri mwa anthuwa amakhala ana obadwira m’banja la Mboni ndipo amakhala kuti asankha moyo wabwino kwambiri. (Sal. 1:1-3) Ngati ndinu makolo, muyenera kuti mumalakalaka kuona mwana wanu akubatizidwa. (Yerekezerani ndi 3 Yohane 4.) Muyeneranso kuti mumafuna kuti mwana wanu adziwe malemba oyera, omwe masiku ano ndi Malemba Achiheberi komanso Malemba Achigiriki. Ngakhale ana aang’ono akhoza kuphunzira za anthu ena komanso nkhani zina za m’Baibulo. Ndipo gulu la Yehova lapereka zinthu zambiri zimene zingathandize makolo pophunzitsa ana awo. Musaiwale kuti kudziwa Malemba n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. w17.12 18 ¶1; 19 ¶4
Lachitatu, April 10
Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake.—Aef. 5:23.
Ngati ndinu mlongo ndipo mukuona kuti mwamuna wanu yemwe si Mboni sachita bwino zinthu, kodi mungatani? Kodi kukangana naye pa nkhani zimene amalakwitsa kungathandize kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino? Ngakhale zitatheka kuti asinthe n’kumachita zimene inuyo mumafuna, n’zokayikitsa kuti angayambe kuphunzira Baibulo. Koma mukamayesetsa kumulemekeza, mudzathandiza kuti m’banja mwanu mukhale mtendere ndipo mudzalemekeza kwambiri Yehova. N’kuthekanso kuti mwamunayo akhoza kuyamba kuphunzira ndipo pamapeto pake nonse mudzalandira mphoto. (1 Pet. 3:1, 2) Ngati ndinu m’bale ndipo mukuona kuti mkazi wanu yemwe si Mboni sakulemekezani, kodi mungatani? Kodi kumukalipira kuti adziwe zoti ndinu mutu kungathandize kuti ayambe kukulemekezani? Yankho ndi lakuti ayi. Paja Mulungu amanena kuti amuna ayenera kutsanzira Yesu n’kumatsogolera banja lawo mwachikondi. Yesu amatsogolera mpingo mwachikondi komanso moleza mtima. (Luka 9:46-48) Mwamuna akamatsanzira Yesu akhoza kuthandiza mkazi wake kuti nayenso ayambe kulambira Yehova. w17.11 28-29 ¶13-14
Lachinayi, April 11
Amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.—Aheb. 3:4.
Maganizo a m’dzikoli amachititsa anthu kuona kuti malangizo a Yehova ndi osathandiza ndipo zimenezi zikhoza kufooketsa chikhulupiriro cha munthu. Masiku ano maganizo amenewa ali paliponse ndipo amalimbikitsidwa pa TV, pa intaneti, kuntchito komanso kusukulu. M’mayiko ena anthu ambiri sakhulupirira Mulungu ndipo amanena kuti sangalowe chipembedzo chilichonse. N’kutheka kuti sanafufuze kuti adziwe ngati kuli Mulungu kapena ayi. Chimene amangofuna n’kukhala ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna. (Sal. 10:4) Anthu ena amaona ngati ndi nzeru kunena kuti, “Ndikhoza kukhala ndi makhalidwe abwino popanda kukhulupirira Mulungu.” Kodi pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti kulibe Mulungu? Munthu akafufuza zimene asayansi amanena kuti adziwe ngati zamoyo zinachita kulengedwa kapena ayi, akhoza kusokonezedwa ndi mfundo zambirimbiri. Koma kunena zoona, kupeza yankho lake n’kosavuta. Kuti nyumba ikhalepo pamafunika munthu woti aimange, ndiye kuli bwanji zinthu zamoyo? w17.11 20-21 ¶2-4
Lachisanu, April 12
Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.—Mal. 3:16.
Tiyenera kuganizira kufunika kopezeka pa Chikumbutso. Tizikumbukira kuti tikamasonkhana timakhala kuti tikulambira Yehova. Choncho Yehova ndi Yesu ayenera kuti amayamikira anthu amene amayesetsa kuti afike pamsonkhano wofunika kwambiri wa Chikumbutso. Timafuna kuti iwo aone kuti timayesetsa kupezeka pamsonkhanowu kupatulapo ngati pali mavuto aakulu. Tiyenera kusonyeza kuti timaona kuti misonkhano yathu ndi yofunika kwambiri. Izi zimathandiza kuti Yehova asunge dzina lathu ‘m’buku la chikumbutso’ kapena kuti “m’buku la moyo.” Bukuli ndi limene iye amalembamo mayina a anthu amene adzapeze moyo wosatha. (Chiv. 20:15.) Chikumbutso chikamayandikira, tingachite bwino kupeza nthawi yoti tizipemphera komanso kuganizira bwinobwino za ubwenzi wathu ndi Yehova.— 2 Akor.13:5. w18.01 13 ¶4-5
Loweruka, April 13
Azithawira kumzinda umodzi mwa mizindayi.—Yos. 20:4.
Munthu akakhala mumzinda wothawirako, ankakhala wotetezeka. Paja Yehova anati: “Mizindayo ntchito yake ikhale yoti wopha munthu mwangozi azithawirako pothawa wobwezera magazi.” (Yos. 20:2, 3) Yehova sankalola kuti munthu aimbidwe mlandu kawiri pa tchimo limodzi komanso kuti wobwezera magazi apite kukapha munthu amene walowa kale mumzinda wothawirako. Izi zinkachititsa munthu amene wathawira mumzindawo kumva kuti ali m’manja mwa Yehova ndipo ndi wotetezeka. Iye sankamva ngati ali kundende. Akakhala mumzindamo ankatha kugwira ntchito, kuthandiza anthu ena komanso kutumikira Yehova mwamtendere. Choncho ankatha kukhalabe ndi moyo wosangalala. Atumiki a Yehova ena amene anachita machimo akuluakulu n’kulapa, amadziimbabe mlandu moti amamva ngati ali m’ndende ndipo amaona kuti Yehova sangawakhululukire. Ngati mumamva choncho, dziwani kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri moti akakhululuka sadzakuimbaninso mlandu pa nkhaniyo. w17.11 9 ¶6; 11-12 ¶13-14
Lamlungu, April 14
Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri Abale akakhala pamodzi mogwirizana.—Sal. 133:1.
Chinthu china chimene chingatithandize kuti tizigwirizana ndi kuganizira zimene zizindikiro za pa Chikumbutso zimaimira. Tsiku la mwambowu lisanafike komanso pa tsikulo, tiyenera kuganizira kwambiri kufunika kwa zimene mkate wopanda chofufumitsa komanso vinyo wofiira zimaimira. (1 Akor. 11:23-25) Mkate umaimira thupi la Yesu lopanda uchimo limene linaperekedwa nsembe ndipo vinyo amaimira magazi ake. Koma chofunika si kungodziwa kuti chizindikiro ichi chimaimira chakuti, ichi chimaimira chakuti. Tizikumbukira kuti dipo ndi njira imene Yehova ndi Yesu anasonyezera chikondi kuposa munthu wina aliyense. Yehova anasonyeza chikondi popereka Mwana wake kuti adzatifere ndipo Yesu anasonyeza chikondi pololera kupereka moyo wake chifukwa cha ifeyo. Kuganizira chikondi chimenechi kungatilimbikitse kuti nafe tiziwakonda. Ndipo chikondi chimene aliyense wa ife ali nacho kwa Yehova chili ngati chingwe chimene chimatimangirira pamodzi kuti tizikhala ogwirizana kwambiri. w18.01 14-15 ¶11
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 dzuwa litalowa) Mateyu 26:6-13
Lolemba, April 15
Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.—1 Yoh. 4:9.
Yehova amakonda anthu kwambiri ndipo amaona kuti ndi amtengo wapatali. N’chifukwa chake analolera kupereka moyo wa Mwana wake kuti tidzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Yehova atapanda kukwaniritsa malonjezo ake, Mdyerekezi angakhale ndi chifukwa chonenera kuti Mulungu ndi wabodza, amatimana zinthu zabwino komanso salamulira mwachilungamo. Nawonso anthu otsutsa Mulungu akhoza kuoneka ngati amanena zoona. Paja amanena kuti: “Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.” (2 Pet. 3:3, 4) Yehova akadzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira adzapulumutsanso anthu omvera. (Yes. 55:10, 11) Mfundo ina yofunika kuikumbukira ndi yakuti ulamuliro wa Yehova ndi wachikondi. Choncho sitiyenera kukayikira kuti nthawi zonse Yehova amakonda anthu ake okhulupirika, amawayamikira ndiponso amawaona kuti ndi ofunika.—Eks. 34:6. w17.06 23-24 ¶7
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Mateyu 21:1-11, 14-17
Lachiwiri, April 16
[Mulungu] anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.—1 Yoh. 4:10.
Kungoyambira pamene Yehova analonjeza zoti adzapulumutsa anthu, mogwirizana ndi lemba la Genesis 3:15, m’maganizo mwake zinali ngati zachitika kale. Patapita zaka pafupifupi 4,000, Yehova analolera kuti Mwana wake aphedwe n’cholinga choti apulumutse anthu. (Yoh. 3:16) Timayamikira kwambiri kuti Yehova analolera kuchita zimenezi ngakhale kuti zinali zopweteka kwambiri. Popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, nafenso tikhoza kusonyeza chikondi chapamwambachi. N’zoona kuti timavutika kusonyeza chikondichi chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu, koma sikuti n’zosatheka. Mwachitsanzo, Abele anasonyeza kuti amakonda Mulungu pamene anasankha zinthu zabwino kwambiri n’kupereka nsembe. (Gen. 4:3, 4) Nowa anasonyezanso chikondi pogwira ntchito youza anthu uthenga wa Mulungu kwa zaka zambiri ngakhale kuti sankamumvera. (2 Pet. 2:5) Nayenso Abulahamu anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Mulungu pololera kuchita zinthu zovuta kwambiri. Iye analolera kuti apereke mwana wake nsembe. (Yak. 2:21) Mofanana ndi anthu okhulupirika amenewa, tiyenera kusonyeza ena chikondi ngakhale kuti si zophweka. w17.10 7-8 ¶3-4
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Mateyu 21:18, 19; 21:12, 13; Yohane 12:20-50
Lachitatu, April 17
Mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.—Aheb. 4:15.
Ntchito ya Mkulu wa Ansembe wathu Yesu imatitsimikizira kuti machimo athu angakhululukidwe komanso kuti ‘adzatichitira chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.’ (Aheb. 4:16) Choncho muyenera kukhulupirira nsembe ya Yesu. Sikuti muzingokhulupirira kuti nsembeyi ikhoza kupulumutsa anthu ambirimbiri. Koma muzikhulupirira kuti nsembeyo ikhoza kukuthandizani inuyo panokha. (Agal. 2:20, 21) Muzikhulupirira kuti dipo limathandiza kuti machimo anu akhululukidwe. Muzikhulupiriranso kuti dipo lingakuthandizeni inuyo kuti mudzapeze moyo wosatha. Nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Yehova anakupatsani inuyo. Masiku anonso, Yehova akatikhululukira sitiyenera kuopa kuti atikumbutsanso nkhaniyo kapena kutiimbanso mlandu. (Sal. 103:8-12) Choncho tisamakayikire kuti Mulungu amakhululuka ndi mtima wonse. w17.11 11-12 ¶14-17
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Mateyu 21:33-41; 22:15-22; 23:1-12; 24:1-3
Lachinayi, April 18
Sindikupemphera awa okha, komanso amene amakhulupirira ine kudzera m’mawu awo, kuti onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana.—Yoh. 17:20, 21.
Usiku umene Yesu anayambitsa mwambowu, anapemphera kuti otsatira ake akhale ogwirizana ngati mmene zilili pakati pa iyeyo ndi Atate wake. Yehova wayankhadi pemphero la Mwana wakeli moti panopa anthu mamiliyoni ambiri akukhulupirira kuti Yesu anatumidwa ndi Yehova. Umboni wakuti a Mboni za Yehovafe ndi ogwirizana umaonekera kwambiri pa Chikumbutso kuposa pamisonkhano yonse imene timakhala nayo. Pa tsiku la mwambowu, anthu a mitundu yosiyanasiyana amasonkhana padziko lonse. Izi n’zochititsa chidwi chifukwa kumadera ena, anthu a mitundu yosiyana sachitira limodzi misonkhano yachipembedzo ndipo amanyoza anthu amene amachita zimenezi. Koma Yehova ndi Yesu amasangalala kwambiri kuona anthu osiyana akusonkhana pamodzi mogwirizana. Anthu a Yehovafe sitidabwa ndi mgwirizano wathu. Paja Yehova ananeneratu kuti tidzakhala ogwirizana.—Ezek. 37:15-17; Zek. 8:23. w18.01 14 ¶7-9
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6
Tsiku la Chikumbutso
Dzuwa Litalowa
Lachisanu, April 19
Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.—Sal. 118:22.
“Omanga nyumba,” kapena kuti atsogoleri achiyuda, anakana Mesiya. Sikuti anangokana kutsatira Yesu kapena kukhulupirira kuti anali Khristu. Ayuda ambiri anafika pofuna kumupha. (Luka 23:18-23) Ndipo iwo ndi amene anachititsa kuti Yesu aphedwe. Ngati Yesu anakanidwa komanso kuphedwa, kodi akanakhala bwanji “mwala wofunika kwambiri wapakona”? Zimenezi zikanatheka pokhapokha ngati akanaukitsidwa. Mtumwi Petulo ananena kuti “Yesu Khristu Mnazareti uja, amene inu munamupachika pamtengo, . . . Mulungu anamuukitsa kwa akufa.” Kenako anati: “Yesu ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’” (Mac. 3:15; 4:5-11; 1 Pet. 2:5-7) Yesu ataphedwa anaukitsidwadi ndipo anapatsidwa udindo wofunika kwambiri wopulumutsa anthu.—Mac. 4:12; Aef. 1:20. w17.12 9-10 ¶6-9
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Mateyu 26:17-19; Luka 22:7-13 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Mateyu 26:20-56
Loweruka, April 20
[Muzilengezabe] imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.—1 Akor. 11:26.
Pofotokoza za chisautso chachikulu chimene chatsala pang’ono kufika, Yesu anati: “Chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba. . . . ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. [Yesu] adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.” (Mat. 24:29-31) Mawu oti “adzasonkhanitsa osankhidwa ake” akunena za nthawi imene odzozedwa onse amene adzatsale ndi moyo padzikoli adzatengedwe kukalandira mphoto yawo kumwamba. Zimenezi zidzachitika mbali yoyamba ya chisautso chachikulu ikadzadutsa koma nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Kenako a 144,000 onse adzathandiza Yesu kuti agonjetse mafumu a dzikoli. (Chiv. 17:12-14) Choncho Chikumbutso chimene chidzachitike odzozedwawa atatsala pang’ono kutengedwa kupita kumwamba chidzakhala chomaliza chifukwa Yesu adzakhala atabwera. w18.01 16 ¶15
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Mateyu 27:1, 2, 27-37
Lamlungu, April 21
Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za choonadi chimenecho.—Mac. 2:32.
Yesu ali kumwamba ndipo adzakhalabe “ndi moyo kwamuyaya.” (Aroma 6:9; Chiv. 1:5, 18; Akol. 1:18; 1 Pet. 3:18) Iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti adzakalamulira limodzi naye kumwamba. (Luka 22:28-30) Paulo analemba kuti: “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” Kenako anasonyeza kuti padzakhala anthu enanso amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akor. 15:20, 23) Nthawi ya “kukhalapo” kwa Yesu inayamba mu 1914. Nthawiyi ikupitirira ndipo mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri. w17.12 10-11 ¶11, 14-16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66 (Zochitika pa Nisani 16 dzuwa litalowa) Mateyu 28:2-4
Lolemba, April 22
Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.—Yes. 51:12.
Nayenso Atate wathu wachifundo anaona anthu amene ankawakonda akumwalira ndipo ena a iwo anali Abulahamu, Isaki, Yakobo, Mose ndiponso Davide. (Num. 12:6-8; Mat. 22:31, 32; Mac. 13:22) Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Yehova akufunitsitsa kwambiri kuti adzawaukitse. (Yobu 14:14, 15) Anthu amenewa akadzaukitsidwa adzakhala osangalala komanso athanzi. Tisaiwalenso kuti Mwana wokondedwa wa Mulungu, yemwe ‘ankasangalala naye,’ anafa imfa yopweteka kwambiri. (Miy. 8:22, 30) Pa nthawi imeneyi, Yehova ayenera kuti anamva kupweteka kosaneneka. (Yoh. 5:20; 10:17) Sitiyenera kukayikira kuti Yehova angatithandize ngati taferedwa. Choncho tiyenera kupemphera kwa iye n’kumuuza mmene tikumvera mumtima mwathu. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa chisoni chathu ndipo angatilimbikitse m’njira yoyenerera.—2 Akor. 1:3, 4. w17.07 13 ¶3-5
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Mateyu 28:1, 5-15
Lachiwiri, April 23
Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.—Aheb. 6:10.
Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri ayamba kulambira Yehova ndipo iwo amapereka ndi mtima wonse ‘zinthu zawo zamtengo wapatali’ monga nthawi, mphamvu komanso chuma kuti azithandiza pakachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Miy. 3:9) Zimene timachita posonyeza kuti timakonda Yehova sizidzaiwalika. M’masiku otsiriza ano, anthu a Yehova achita zinthu zazikulu kwambiri zomwe zikusonyeza kuti Yehova akuwadalitsa komanso Khristu akuwatsogolera. Gulu lathu ndi lotetezeka kwambiri komanso lidzakhalapo mpaka kalekale. Tiziyamikira kwambiri kuti tili m’gulu la Yehova ndipo tisasiye ‘kumvera mawu a Yehova Mulungu wathu.’ Tikatero, Mfumu yathu yomwenso ndi Mkulu wa Ansembe adzapitiriza kutiteteza. Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe pothandiza kuti kulambira koona kuziyenda bwino. Tikamachita zimenezi, Yehova wa makamu adzatiteteza nthawi imene yatsala m’dziko loipali ndipo sadzatisiya mpaka kalekale. w17.10 30 ¶18-19
Lachitatu, April 24
Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama, kuti chumacho chikatha, akakulandireni m’malo okhala amuyaya.—Luka 16:9.
Posachedwapa, mbali zonse za dziko la Satanali, zomwe ndi andale, achipembedzo komanso amalonda zidzatheratu. Mneneri Ezekieli ndi Zefaniya ananeneratu kuti golide ndi siliva zimene amalonda akhala akugwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali zidzakhala zopanda ntchito. (Ezek. 7:19; Zef. 1:18) Kodi munthu angamve bwanji ataona kuti watsala pang’ono kufa kenako n’kuzindikira kuti walephera kupeza chuma chenicheni chifukwa choti ankatanganidwa ndi kufunafuna “chuma chosalungama”? Zikhoza kufanana ndi munthu amene wakhala akugwira ntchito kwa moyo wake wonse kuti apeze ndalama zambirimbiri koma n’kuzindikira kuti ndalama zonsezo n’zachinyengo. (Miy. 18:11) Popeza n’zosakayikitsa kuti chuma cha m’dzikoli chidzatha, tiyeni tiyesetse kuchigwiritsa ntchito mwanzeru kuti ‘tipeze mabwenzi’ kumwamba. Chilichonse chimene timachita chothandiza pa ntchito za Ufumu wa Yehova chimachititsa kuti tikhale olemera mwauzimu. w17.07 11 ¶16
Lachinayi, April 25
Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi, monganso Khristu anakukondani n’kudzipereka yekha chifukwa cha inu.—Aef. 5:1, 2.
Akhristu ena amene anachita tchimo lalikulu amabisa poopa kuti achita manyazi kapena akhumudwitsa anthu ena. (Miy. 28:13) Munthu amene amabisa machimo si wachikondi chifukwa zimenezi sizimangosokoneza iyeyo koma zimasokonezanso anthu ena. Zikhoza kulepheretsa mzimu woyera kuti uzigwira ntchito bwino mumpingo ndipo zingasokonezenso mtendere mumpingo. (Aef. 4:30) Munthu amene ali ndi chikondi chenicheni akachita tchimo lalikulu, amauza akulu kuti amuthandize moyenera. (Yak. 5:14, 15) Pa makhalidwe onse abwino, khalidwe lalikulu kwambiri ndi chikondi. (1 Akor. 13:13) Tikakhala achikondi timasonyeza kuti timatsatira Khristu komanso timatsanzira Yehova yemwe anayambitsa chikondi. Paulo analemba kuti ngati “ndilibe chikondi, sindili kanthu.” (1 Akor. 13:2) Choncho tiyeni tonse tipitirize kusonyeza “chikondi chenicheni m’zochita zathu” osati “ndi mawu okha.”—1 Yoh. 3:18. w17.10 11 ¶17-18
Lachisanu, April 26
Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.—Mac. 5:29.
Yosefe anasonyeza kulimba mtima pamene mkazi wa Potifara ankamunyengerera kuti agone naye. Yosefe ayenera kuti ankadziwa kuti akakana zinthu sizingamuyendere bwino. Ngakhale zinali choncho, iye analimba mtima ndipo anakana. (Gen. 39:10, 12) Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Rahabi. Iye sanachite mantha pamene Aisiraeli ena anabwera kudzazonda mzinda wa Yeriko. Chifukwa chakuti Rahabi anadalira Yehova, iye analimba mtima n’kubisa Aisiraeliwo m’nyumba yake ndipo kenako anawathandiza kuti athawe. (Yos. 2:4, 5, 9, 12-16) Atumwi okhulupirika ankaona zimene Yesu ankachita posonyeza kulimba mtima ndipo zimenezi zinawathandiza kuti nawonso akhale olimba mtima. Pamene Asaduki ankawatsutsa, atumwiwo sanasiye kuphunzitsa za Yesu. (Mac. 5:17, 18, 27-29) Kulimba mtima kunathandiza Yosefe, Rahabi, Yesu ndiponso atumwi kuti achite zinthu zoyenera. Sikuti ankalimba mtima chifukwa chodzidalira koma chifukwa chodalira Yehova. Nafenso timafunika kulimba mtima pa nkhani zosiyanasiyana. Koma m’malo modzidalira, tiyenera kudalira Yehova.—2 Tim. 1:7. w17.09 29 ¶6-9
Loweruka, April 27
Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.—Akol. 3:9.
Anthufe patokha sitingakwanitse kuvula umunthu wakale. Anthu amene anachita zimenezi anavutika kwambiri kuti asiye makhalidwe awo oipa. Koma anakwanitsa chifukwa cholola kuti Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera ziwathandize kusintha maganizo ndi mitima yawo. (Luka 11:13; Aheb. 4:12) Kuti nafenso tivule umunthu wakale, tiyenera kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kusinkhasinkha komanso kupempha Mulungu nthawi zonse kuti atipatse nzeru ndi mphamvu zotithandiza kutsatira malangizo a m’Baibulo. (Yos. 1:8; Sal. 119:97; 1 Ates. 5:17) Kukonzekera misonkhano komanso kupezekapo zimathandizanso kuti tizitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera. (Aheb. 10:24, 25) Tiyenera kugwiritsanso ntchito njira zosiyanasiyana zimene gulu la Yehova limaperekera chakudya chauzimu masiku ano. (Luka 12:42) N’zoona kuti Akhristu ayenera kuvula umunthu wakale, koma zofunika kuti tisangalatse Mulungu si zokhazi. Tiyeneranso kuvala umunthu watsopano.—Akol. 3:10. w17.08 21 ¶16-17
Lamlungu, April 28
Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha. Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu.—Sal. 13:5.
Davide anachitiridwa zinthu zambiri zopanda chilungamo. Ngakhale kuti Yehova anamudzoza ali wamng’ono kuti adzakhale mfumu, iye anadikira kwa zaka 15 kuti ayambe kulamulira fuko lake. (2 Sam. 2:3, 4) Pa nthawi yodikirayi, Sauli, yemwe anali mfumu yosakhulupirika, ankamusakasaka kuti amuphe. Izi zinachititsa kuti Davide azingothawathawa, kubisala m’mapanga a m’chipululu ndiponso nthawi zina ankakhala kudziko lina. Sauliyo ataphedwa kunkhondo, Davide anadikiranso zaka zina pafupifupi 7 kuti ayambe kulamulira mtundu wonse wa Isiraeli. (2 Sam. 5:4, 5) Kodi n’chifukwa chiyani Davide anayembekezera moleza mtima? Iye ankakhulupirira kuti Yehova ndi wokoma mtima kwambiri. Choncho sanakhumudwe koma ankayembekezera kuti Yehova adzamupulumutsa ndipo ankaganizira zinthu zabwino zimene Yehovayo anamuchitira. (Sal. 13:6) Davide ankadziwa ubwino wodikira moleza mtima. w17.08 6-7 ¶14-15
Lolemba, April 29
Mulungu alibe tsankho.—Mac. 10:34.
Pakapita nthawi, zilankhulo zimasintha moti matanthauzo a mawu ena amasinthiratu. Mwina mwaona zimenezi m’chilankhulo china chimene mumachidziwa. Umu ndi mmene zilili ndi Chiheberi komanso Chigiriki. Pafupifupi Baibulo lonse linalembedwa m’zilankhulo ziwirizi. Koma zilankhulo zimenezi zasintha kwambiri masiku ano tikayerekeza ndi mmene zinalili pamene Baibulo linkalembedwa. Choncho anthu ambiri, ngakhale amene amalankhula Chiheberi kapena Chigiriki cha masiku ano, ayenera kuwerenga Baibulo limene linachita kumasuliridwa kuti alimvetse bwino. Anthu ena amaganiza kuti ayenera kuphunzira Chiheberi ndi Chigiriki chakale n’cholinga choti aziwerenga Baibulo m’chilankhulo chimene linalembedwa. Koma zimenezi sizingawathandize kwenikweni. Chosangalatsa n’chakuti panopa Baibulo lathunthu kapena mbali zake zina zamasuliridwa m’zilankhulo zoposa 3,000. Apa zikuonekeratu kuti Yehova amafuna kuti Mawu ake azithandiza anthu ochokera ‘kudziko lililonse, fuko lililonse komanso chinenero chilichonse.’ (Chiv. 14:6) Kudziwa zimenezi kumatilimbikitsa kukonda kwambiri Mulungu wathu yemwe ndi wopanda tsankho. w17.09 19 ¶4
Lachiwiri, April 30
Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu, ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.—Miy. 17:27.
Ngati muli ndi achibale amene anachotsedwa mungafunike kudziletsa kuti musamalankhule nawo popanda chifukwa chomveka. Kukumbukira kuti mukuchita zimenezi chifukwa chomvera malangizo a Mulungu komanso kutsatira chitsanzo chake kungakuthandizeni kwambiri. Chitsanzo chabwino cha kudziletsa ndi Mfumu Davide. Ngakhale kuti anali ndi mphamvu, sanachite zinthu mopupuluma kuti abwezere zimene Sauli ndi Simeyi anamuchitira. (1 Sam. 26:9-11; 2 Sam. 16:5-10) Koma sikuti Davide ankadziletsa nthawi zonse. Paja anachita chigololo ndi Batiseba komanso atanyozedwa ndi Nabala anatsala pang’ono kupha anthu. (1 Sam. 25:10-13; 2 Sam. 11:2-4) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Davide? Choyamba, oyang’anira m’gulu la Mulungu ayenera kusamala kwambiri kuti asamagwiritse ntchito molakwika udindo wawo. Chachiwiri, palibe munthu amene sangayesedwe.—1 Akor. 10:12. w17.09 5-6 ¶12-13