March
Lachisanu, March 1
Modzichepetsa [muziona] ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.
Kodi mumpingo wanu muli munthu wina amene zochita zake sizikusangalatsani? Zimakhala zovuta kuti muzikonda munthu wotereyu ndipo ngati simuchitapo kanthu, maganizo amenewa sangakuthereni. Koma Baibulo limanena kuti kuchereza anthu, ngakhale adani athu, kumathandiza kuti tizigwirizana nawo. (Miy. 25:21, 22) Kuchereza munthu kungathandize kuti tiyambe kugwirizana naye. Zikhoza kuthandiza kuti tiyambe kuona makhalidwe ake abwino amene anachititsa kuti Yehova amukokere m’gulu lake. (Yoh. 6:44) Chikondi chikakulimbikitsani kuitana munthu amene simunkagwirizana naye poyamba zingathandize kuti muyambe kugwirizana. Ndiye kodi mungadziwe bwanji kuti mukuitana munthu chifukwa cha chikondi? Chinthu china chimene chingatithandize ndi kutsatira malangizo amulemba la lero. Tikamaganizira zinthu zimene ena amachita bwino kuposa ifeyo, tingayambe kuwakonda kwambiri komanso kufuna kuwachereza. Anthuwa angatipose pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro, kupirira, kulimba mtima kapena makhalidwe ena. w18.03 17 ¶18-19
Loweruka, March 2
[Yehova] safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe.—2 Pet. 3:9.
Chikhulupiriro cha makolo ena chimayesedwa mwana wawo akachotsedwa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene mwana wake wamkazi anachotsedwa n’kuchoka pakhomo. Mlongoyu anati: “Ndinkayesetsa kufufuza zifukwa m’mabuku athu zondichititsa kuti ndizichezabe ndi mwana wanga komanso chidzukulu changa. Koma mwamuna wanga anandithandiza mokoma mtima kuzindikira kuti pa nthawiyo mwana wathu sanalinso m’manja mwathu choncho tisadzilowetse m’mavuto.” Patapita zaka zingapo, mwana wawoyo anabwezeretsedwa. Mlongoyu anati: “Makolofe amatilemekeza kwambiri chifukwa choti tinayesetsa kumvera Mulungu. Kunena zoona timagwirizana kwambiri.” Ngati mwana wanu wachotsedwa, kodi ‘mudzakhulupirira Yehova ndi mtima wanu wonse n’kumapewa kudalira luso lanu lomvetsa zinthu?’ (Miy. 3:5, 6) Choncho musamakayikire malangizo komanso chilango chake. Muzimvera Yehova ngakhale pamene kuchita zimenezi n’kopweteka kwambiri. Tiyeni tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehova osati motsutsana nawo. w18.03 31 ¶12-13
Lamlungu, March 3
Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.—Mat. 28:19.
Baibulo silinena kuti munthu amafunika kubatizidwa akafika zaka zinazake. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kuphunzitsa munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu’ pa Mateyu 28:19 amatanthauza kuphunzitsa munthu n’cholinga choti akhale wophunzira. Ndipo wophunzira ndi munthu amene amaphunzira komanso kumvetsa zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo amafunitsitsa kuti azitsatira zimene ankaphunzitsazo. Choncho cholinga cha makolo chiyenera kukhala kuphunzitsa ana awo kuyambira ali aang’ono kwambiri mpaka anawo atakhala ophunzira obatizidwa a Khristu. N’zoona kuti khanda siliyenera kubatizidwa. Koma Baibulo limasonyeza kuti ngakhale ana aang’ono akhoza kumvetsa ndiponso kuyamikira mfundo zoona za m’Baibulo. Mwachitsanzo, Timoteyo anali Mkhristu amene anayamba kukonda choonadi ali wamng’ono. Iye anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri. (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) Timoteyo asanakwanitse zaka za m’ma 20 kapena atapitirira pang’ono, anali atakhala Mkhristu woyenerera kulandira maudindo apadera mumpingo.—Mac. 16:1-3. w18.03 9 ¶4-5
Lolemba, March 4
Munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.—Aef. 4:23.
Anthufe titayamba kutumikira Yehova tinasintha zinthu zambiri pa moyo wathu. Kusinthaku kunapitirizabe ngakhale titabatizidwa. Popeza tonsefe si angwiro, tiyenera kupitiriza kusintha zinthu zina. (Afil. 3:12, 13) Kuti tipitirize kukula mwauzimu tiyenera kudzifufuza moona mtima. Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti ndikusintha n’kukhala munthu wolimba mwauzimu? Kodi ndikumatsanzira kwambiri Khristu? Nanga zimene ndimachita ndikakhala kumisonkhano zimasonyeza kuti moyo wanga wauzimu uli bwanji? Kodi zimene ndimakonda kukambirana ndi anthu ena zimasonyeza kuti ndimalakalaka chiyani? Nanga zimene ndimachita pa nkhani yophunzira Baibulo, kavalidwe komanso kudzikongoletsa zimasonyeza kuti ndine munthu wotani? Kodi ndimatani ndikapatsidwa malangizo kapena ndikakumana ndi mayesero? Nanga kodi ndasintha kuchoka pongodziwa mfundo zoyambirira n’kufika pokhala Mkhristu wolimba mwauzimu?’ (Aef. 4:13) Kuganizira zimene tingayankhe pa mafunso amenewa kungatithandize kudziwa ngati tikukula mwauzimu. w18.02 24 ¶4-5
Lachiwiri, March 5
Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.—Sal. 144:15.
Tikukhala mu nthawi yapadera kwambiri. Mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo, Yehova akusonkhanitsa “khamu lalikulu la anthu . . . lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” Anthu amene asonkhanitsidwa ndi “mtundu wamphamvu” wa anthu osangalala oposa 8 miliyoni, omwe “akumuchitira [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Chiv. 7:9, 15; Yes. 60:22) Apa zikuonekeratu kuti masiku ano pali anthu ambiri amene amakonda Mulungu komanso anzawo. Komatu Malemba ananeneratu kuti masiku otsiriza ano, anthu amene satumikira Mulungu adzakhala okonda zinthu zongowakomera okha. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘M’masiku otsiriza anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama ndiponso okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.’ (2 Tim. 3:1-4) Zinthu zimene anthuwa amakonda n’zosemphana kwambiri ndi zimene Akhristu amayenera kukonda. Ndipo anthu oterewa ndi amene amachititsa kuti nthawi yathuyi ikhale “yovuta.” w18.01 22-23 ¶1-2
Lachitatu, March 6
Amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.—Miy. 28:5.
Kudziwa bwino Mulungu kunathandiza Nowa kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso nzeru yochokera kwa Mulungu. Zimenezi zinamuthandizanso kuti asamachite chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Mwachitsanzo, popeza Nowa ‘ankayenda ndi Mulungu woona,’ sankayenda kapena kucheza ndi anthu oipa. Anthu opanda chikhulupiriro ankagometsedwa ndi mphamvu za ziwanda zimene zinabwera padzikoli ngati anthu ndipo mwina anafika pomalambira ziwandazo. Koma Nowa sanapusitsidwe ndi ziwandazi. (Gen. 6:1-4, 9) Nowa ankadziwa kuti anthu ndi amene anauzidwa kuti aberekane n’kudzaza dziko lapansi. (Gen. 1:27, 28) Choncho ayenera kuti ankadziwa kuti kugonana pakati pa akazi ndi angelo oipa ndi kosayenera. Mfundo imeneyi inaonekeratu pamene kunabadwa ana amene anali aakulu komanso amphamvu mwachilendo. Patapita nthawi, Mulungu anachenjeza Nowa kuti adzabweretsa chigumula padziko lapansi. Nowa ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo anamanga chingalawa chomwe iye ndi banja lake anapulumukiramo.—Aheb. 11:7. w18.02 9-10 ¶8
Lachinayi, March 7
Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.—1 Akor. 15:10.
Ngati mwachita tchimo lalikulu, Yehova amafunitsitsa kuti akuthandizeni kukhalanso naye pa ubwenzi. Koma muyenera kugwiritsa ntchito njira zimene Yehova wapereka kudzera mumpingo. (Miy. 24:16; Yak. 5:13-15) Musazengereze pochita zimenezi chifukwa mukatero mukhoza kulephera kudzalandira moyo wosatha. Koma kodi mungatani ngati pambuyo pokhululukidwa tchimo linalake, mukudziimbabe mlandu? Nayenso Paulo nthawi zina ankadandaula chifukwa cha zinthu zimene analakwitsa m’mbuyomu. Iye ananena kuti: “Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” (1 Akor. 15:9) Yehova ankakonda Paulo mmene analili ndipo ankafuna kuti nayenso aziona chimodzimodzi. Ngati mwalapa machimo amene munachita m’mbuyomu ndipo mwawaulula kwa anthu oyenerera, musamakayikire kuti Yehova adzakuchitirani chifundo. Choncho muzikhulupirira kuti Yehova wakukhululukirani monga mmene analonjezera.—Yes. 55:6, 7. w18.01 11 ¶17-18
Lachisanu, March 8
Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.—Yak. 4:8.
Kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Yehova pamafunika kumvetsera mawu ake komanso kulankhula naye. Timamvetsera mawu a Yehova makamaka tikamaphunzira Baibulo patokha. Timachita zimenezi powerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso mabuku ofotokoza Baibulo. Koma tizikumbukiranso kuti pophunzira Baibulo tisamakhale ngati munthu amene akungofuna kuloweza zinazake kuti adzakhoze mayeso. Tizikhala ngati munthu amene ali pa ulendo wopita kudera lachilendo n’cholinga choti akafufuze zinthu zochititsa chidwi. Mukamafufuza mfundo zatsopano zokhudza Yehova mudzatha kumuyandikira ndipo iye adzakuyandikiraninso. Gulu la Yehova latipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuti tizipindula pophunzira Baibulo. Mwachitsanzo, pawebusaiti yathu pali nkhani zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” zimene zingakuthandizeni pophunzira. Nkhani zimenezi zikhoza kukuthandizani kuti musamakayikire zimene mumakhulupirira.—Sal. 119:105. w17.12 25 ¶8-9
Loweruka, March 9
Sizidzavulazana kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera.—Yes. 11:9.
Ulosiwu umanena kuti nyama zidzakhala mwamtendere chifukwa “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” Popeza nyama sizingaphunzire za Yehova, ndiye kuti ulosiwu ukunenanso za kusintha kwa anthu. (Yes. 11:6, 7) Pali anthu ambiri omwe anali oopsa ngati mimbulu koma tsopano amakhala mwamtendere ndi ena. Mungawerenge za ena mwa anthuwa munkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” zomwe zimapezeka pa jw.org. Anthu ena amene poyamba anali oopsa anavala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aef. 4:23, 24) Anthu akamaphunzira zokhudza Mulungu, amayesetsa kuti moyo wawo ugwirizane ndi zimene Mulungu amafuna. Choncho amasintha zimene amakhulupirira, zimene amaganiza komanso khalidwe lawo. Zinthu zimenezi n’zovuta kusintha koma zimatheka chifukwa mzimu wa Mulungu umathandiza anthu amene akufunitsitsa kuchita zimene Mulunguyo amafuna. w18.01 31 ¶15-16
Lamlungu, March 10
Aliyense [adzapatsidwa moyo] pamalo pake.—1 Akor. 15:23.
Ponena za anthu amene adzapite kumwamba, Baibulo limanena kuti iwo adzauka mwadongosolo, “aliyense pamalo pake.” Sitikukayikira kuti anthu ouka padzikoli adzaukanso mwadongosolo. Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi koma imabweretsa mafunso ambiri. Kodi anthu amene adzafe Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu utatsala pang’ono kuyamba, ndi amene adzayambe kuuka n’cholinga choti adzalandiridwe ndi anthu amene akuwadziwa? Nanga kodi atumiki okhulupirika akale amene ali ndi luso lotha kutsogolera anthu adzauka msanga n’cholinga choti adzathandize anthu a Mulungu kukhala mwadongosolo m’dziko latsopano? Kodi anthu amene sanatumikirepo Yehova adzauka pa nthawi iti, nanga adzaukira kuti? Koma kodi pali chifukwa choti tiziswa mitu kuganizira kwambiri mafunso amenewa? Kunena zoona ndi bwino kungoyembekezera n’kudzaona mmene Yehova adzayendetsere zinthu pa nthawi imeneyo. Chofunika panopa n’kuyesetsa kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova amene watilonjeza kudzera mwa Yesu kuti anthu onse amene akuwakumbukira adzauka.—Yoh. 5:28, 29; 11:23. w17.12 12 ¶20-21
Lolemba, March 11
Inu akazi, muzigonjera amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. Inu amuna, musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri. Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse.—Akol. 3:18-20.
Inunso mungavomereze kuti malangizo amene Paulo anaperekawa ndi othandizadi kwa amuna, akazi komanso ana. Baibulo limalangiza amuna kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.” Mwamuna wachikondi amalemekeza mkazi wake pomvetsera maganizo ake komanso kumutsimikizira kuti amaona kuti maganizo akewo ndi ofunika. (1 Pet. 3:7) N’zoona kuti si nthawi zonse pamene angachite zimene mkaziyo wanena, koma kumva maganizo ake kumathandiza kuti asankhe zinthu mwanzeru. (Miy. 15:22) Mwamuna wachikondi amayesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize mkazi wake kuti azimulemekeza, osati kungomulamula kuti azimulemekeza. Mwamuna amene amakonda mkazi wake ndiponso ana ake, amathandiza banja lake kuti lizitumikira Yehova mosangalala komanso kuti lidzalandire mphoto. w17.11 28 ¶12; 29 ¶15
Lachiwiri, March 12
Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake . . . [cha] m’dzikoli.—Akol. 2:8.
Zikuoneka kuti mtumwi Paulo analemba kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Kolose nthawi yoyamba imene anali m’ndende ku Roma koma atatsala pang’ono kutuluka mu 60 kapena 61 C.E. Iye anawafotokozera ubwino womvetsa “zinthu zauzimu.” (Akol. 1:9) Kenako Paulo ananena kuti: “Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakunyengeni ndi mfundo zokopa. Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.” (Akol. 2:4, 8) Paulo anapitiriza kufotokoza chifukwa chake maganizo ena ofala pa nthawiyo anali olakwika komanso zimene zikanachititsa kuti anthu akopeke nawo. Mwachitsanzo, maganizo amenewa angachititse anthu kudziona kuti ndi anzeru komanso apamwamba kuposa ena. Choncho cholinga cha kalata yake chinali kuthandiza abale kuti apewe maganizo a m’dzikoli komanso makhalidwe oipa.—Akol. 2:16, 17, 23. w17.11 20 ¶1
Lachitatu, March 13
Ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule ndi kulitaya kutali.—Mat. 18:8.
Kodi Mkhristu angafunike kudzimana zinthu ziti ngati akufuna kuchitiridwa chifundo ndi Mulungu? Nthawi zina ayenera kudzimana zinthu zimene amakonda kwambiri ngati zinthuzo zingamuchimwitse. (Mat. 18:9) Mwachitsanzo, ngati anzanu ena amakulimbikitsani kuchita zinthu zimene Yehova sasangalala nazo, kodi mungapitirize kucheza nawo? Ngati muli ndi vuto pa nkhani ya mowa, kodi mumapeweratu chilichonse chimene chingakuchititseni kumwa mopitirira malire? Ngati zimakuvutani kuti musamalakelake zachiwerewere, kodi mumapewa mafilimu, mawebusaiti kapena zinthu zina zimene zingakuchititseni kuganizira zogonana? Tizikumbukira ubwino wodzimana chilichonse chimene chingatilepheretse kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Tikutero chifukwa palibe chinthu chimene chimapweteka kwambiri kuposa kusiyidwa ndi Yehova. Komanso palibe chabwino kwambiri kuposa kudziwa kuti Yehova adzatisonyeza “kukoma mtima kosatha mpaka kalekale.”—Yes. 54:7, 8. w17.11 11 ¶12
Lachinayi, March 14
Ili ndi temberero limene likubwera . . . chifukwa aliyense amene akuba sakulandira chilango.—Zek. 5:3.
Lemba la Zekariya 5:4 lanena kuti ‘temberero lidzalowa m’nyumba ya munthu wakuba n’kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo.’ Izi zikusonyeza kuti chiweruzo cha Yehova sichithawika ngakhale munthu atadzikiyira m’nyumba. Chikhoza kufika paliponse pamene munthu wabisala n’kuchititsa kuti zoipa zimene wachita ziululike. Ngakhale munthu wakuba atayesetsa kuti zisadziwike kwa olamulira, mabwana ake, akulu kapena makolo ake, sangabisire Yehova chifukwa iye amatitsimikizira kuti adzaonetsetsa kuti wakuba aliyense wadziwika. (Aheb. 4:13) Zimakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi anthu amene amayesetsa “kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheb. 13:18) Yehova amanyansidwa ndi kuba kwa mtundu uliwonse. Ifeyo timaona kuti ndi mwayi waukulu kutsatira mfundo zake komanso kukhala ndi makhalidwe amene sanganyozetse dzina lake. Tikamachita zimenezi timapewa chiweruzo chimene Yehova adzapereke kwa anthu amene amaphwanya malamulo ake mwadala. w17.10 22 ¶6-7
Lachisanu, March 15
Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.—Aef. 4:3.
Tiyenera kuyesetsa kukhala mwamtendere ndi anzathu ngakhale pamene tikuona kuti sanatimvetse kapena sanatichitire zinthu mwachilungamo. (Aroma 12:17, 18) Kupepesa kumathandiza kuti mtima wa munthu amene wakhumudwa ukhale m’malo, koma kupepesako kuyenera kukhala kochokera mumtima. Mwachitsanzo, m’malo mongonena kuti, “Pepani kuti mwakhumudwa,” ndi bwino kuvomereza zimene talakwitsa ponena kuti, “Pepani kuti zimene ndinanena zija zakukhumudwitsani.” Mtendere ndi wofunika kwambiri makamaka m’banja. Si bwino kuti mwamuna ndi mkazi akakhala pa gulu azinamizira kuti amakondana koma akakhala kwaokha n’kumangokhala osalankhulana, kulankhulana mawu achipongwe kapena kuchitirana nkhanza. Tiyeneranso kukhululuka ndi mtima wonse. Munthu wina akatilakwira tiyenera kumukhululukira ndipo tisamamusungire chakukhosi. Kuti tikhululukire munthu ndi mtima wonse tiyenera kusamala ndi zimene timaganiza n’cholinga choti ‘tisamusungire zifukwa.’ (1 Akor. 13:4, 5) Vuto ndi lakuti tikamasungira Akhristu anzathu zifukwa tikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi anzathuwo komanso ndi Yehova.—Mat. 6:14, 15. w17.10 10-11 ¶14-15
Loweruka, March 16
Mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.—Zek. 6:15.
Kodi Ayuda anamva bwanji atamva uthenga wa Zekariya? Yehova anawatsimikizira kuti awathandiza komanso kuwateteza pa ntchito yomanga kachisi. Mfundo imeneyi iyenera kuti inalimbikitsa kwambiri anthu amene anataya mtima. Koma kodi zikanatheka bwanji kuti anthu ochepa agwire bwinobwino ntchitoyi? Mawu ena amene Zekariya ananena anawalimbikitsa kwambiri pa nkhaniyi. Kuwonjezera pa anthu okhulupirika monga Heledai, Tobiya ndi Yedaya, Mulungu ananena kuti padzakhala anthu ena ambiri omwe “adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.” Yehova atawatsimikizira zimenezi, Ayuda anayambanso mwamsanga kumanga kachisi ngakhale kuti ntchitoyo inali italetsedwa ndi mfumu ya Perisiya. Kuletsa ntchito yomanga kachisi kunali vuto lalikulu kwambiri koma Yehova analithetsa ndipo Ayudawo anamaliza ntchitoyi mu 515 B.C.E. (Ezara 6:22; Zek. 4:6, 7) Koma mawu a Yehova a pa Zekariya 6:15 akufotokozanso zinthu zazikulu kwambiri zomwe zikuchitika masiku ano. w17.10 29-30 ¶17
Lamlungu, March 17
Limba mtima, ugwire ntchitoyi.—1 Mbiri 28:20.
Solomo anauzidwa kuti ayang’anire ntchito yaikulu kwambiri yomanga kachisi ku Yerusalemu. Iye anauzidwa kuti nyumbayo iyenera kudzakhala “yokongola, yaulemerero wosaneneka ndiponso yotchuka ndi yotamandika kumayiko onse.” Koma chofunika kwambiri chinali chakuti kachisiyo anali “nyumba ya Yehova Mulungu woona.” Yehova ndi amene anasankha Solomo kuti ayang’anire ntchitoyi. (1 Mbiri 22:1, 5, 9-11) Davide ankadziwa kuti Mulungu adzathandiza pa ntchitoyi koma ankaona kuti Solomo anali wamng’ono komanso wosadziwa zambiri. Kodi Solomo akanatha kulimba mtima kuti agwire ntchitoyi? Kapena kodi akanalephera kuigwira chifukwa choti anali wamng’ono? Kuti zinthu ziyende bwino, Solomo anafunika kulimba mtima n’kugwira ntchitoyo. Solomo anafunikadi kulimba mtima chifukwa kupanda kutero akanachita mantha ndipo sakanayamba kugwira ntchitoyi. Zimenezi zikanakhala zoipa kwambiri kusiyana ndi kuyamba ntchitoyo n’kuilephera. Ifenso timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tilimbe mtima n’kumaliza ntchito yathu. w17.09 28 ¶1-2; 29 ¶4-5
Lolemba, March 18
Mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.—Yes. 40:8.
Kodi mukuganiza kuti moyo wanu ukanakhala wotani zikanakhala kuti kulibe Baibulo? Simukanakhala ndi malangizo okuthandizani tsiku lililonse. Simukanapezanso mayankho a mafunso okhudza Mulungu, moyo komanso zimene zidzachitike m’tsogolo. Komanso simukanadziwa zimene Mulungu anachitira anthu m’mbuyomu. Koma chosangalatsa n’chakuti Yehova watipatsa Baibulo lomwe ndi Mawu ake. Ndipo iye amatitsimikizira kuti uthenga umene uli m’Baibulo udzakhalapo mpaka kalekale. M’kalata yake, mtumwi Petulo analemba mawu amene amapezeka pa Yesaya 40:8. N’zoona kuti mawuwo si ofotokoza za Baibulo limene tili nalo panopa koma mfundo yake imagwiranso ntchito ponena za uthenga wa m’Baibulo. (1 Pet. 1:24, 25) Baibulo likhoza kutithandiza makamaka ngati tikuliwerenga m’chilankhulo chimene timamva bwino. Anthu okonda Mawu a Mulungu anazindikira mfundo imeneyi kalekale. Choncho kwa zaka zambiri, anthu ena amtima wabwino akhala akugwira ntchito yomasulira Malemba komanso kuwafalitsa mwakhama ngakhale kuti sizinali zophweka. Zimene ankachitazi zinali zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu choti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Tim. 2:3, 4. w17.09 18-19 ¶1-2
Lachiwiri, March 19
Ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?—Gen. 39:9.
Zimene Yosefe anakumana nazo n’zimenenso achinyamata ambiri amakumana nazo. (Gen. 39:7) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina dzina lake Kim. Anzake ambiri akusukulu ankachita chiwerewere ndipo ankakonda kufotokoza monyadira zimene ankachitazo. Koma Kim sankachita nawo zimenezi. Iye ananena kuti nthawi zina ankasalidwa chifukwa chakuti anali wosiyana kwambiri ndi anzake. Anzakewo ankaonanso kuti iye ndi wotsalira chifukwa choti analibe chibwenzi. Kim ankadziwa kuti munthu akakhala wachinyamata zimamuvuta kudziletsa pa nkhaniyi. (2 Tim. 2:22) Nthawi zambiri anzakewo ankamufunsa ngati n’zoona kuti sanagonepo ndi munthu. Zimenezi zinathandiza kuti Kim akhale ndi mpata wowafotokozera chifukwa chake amadzisunga. Timanyadira kwambiri achinyamata amene amayesetsa kupewa chiwerewere ndipo Yehova amawanyadiranso. w17.09 4 ¶8; 5 ¶10
Lachitatu, March 20
Usapse mtima kuti ungachite choipa.—Sal. 37:8.
Anthu amene amakonda kupsa mtima nthawi zambiri amalankhulanso mawu achipongwe. N’zosachita kufunsa kuti khalidwe limeneli likhoza kuyambitsa mavuto m’banja. M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti tizipewa kupsa mtima, mawu achipongwe komanso kulalata. (Aef. 4:31) N’zomvetsa chisoni kuti anthu amene sapewa makhalidwewa amafika pochitanso chiwawa. Anthu ambiri a m’dzikoli amaona kuti kupsa mtima si nkhani yaikulu koma khalidweli limanyoza Mlengi wathu. Akhristu ambiri anayenera kusiya makhalidwe oipa kuti avale umunthu watsopano. (Akol. 3:8-10) Khalidwe lina limene anthu ayenera kusiya ndi kunama. Anthu ambiri amakonda kunama n’cholinga choti asalipire msonkho wochuluka kapena kuti asaimbidwe mlandu. Koma Yehova ndi “Mulungu wachoonadi.” (Sal. 31:5) Choncho amafuna kuti munthu “aliyense” amene amamulambira ‘azilankhula zoona’ ndipo ‘asamanamize’ anzake. (Aef. 4:25; Akol. 3:9) Choncho tiyenera kunena zoona zokhazokha ngakhale pamene tikuona kuti zingakhale zochititsa manyazi kapena zovuta.—Miy. 6:16-19. w17.08 18 ¶3, 5; 20 ¶12-13, 15
Lachinayi, March 21
Mawu akewo amathamanga kwambiri.—Sal. 147:15.
Masiku ano, Yehova amagwiritsa ntchito Mawu ake opezeka m’Baibulo kuti azititsogolera. Ndipo tinganene kuti “mawu akewo amathamanga kwambiri” chifukwa Yehova amatipatsa malangizo oyenera pa nthawi iliyonse imene tikufunikira malangizowo. Taganizirani za malangizo othandiza amene mumalandira mukamawerenga Baibulo, kuphunzira mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kuonera JW Broadcasting, kupita pa jw.org, kulankhula ndi akulu komanso kucheza ndi Akhristu anzanu. (Mat. 24:45) Muyenera kuti mwaona kuti Yehova sachedwa kukupatsani malangizo othandiza. Wolemba salimo uja ankadziwa kuti Aisiraeli anali ndi mwayi waukulu kwambiri. Zili choncho chifukwa ndi iwo okha amene anapatsidwa “mawu” a Mulungu komanso “malangizo ake ndi zigamulo zake.” (Sal. 147:19, 20) Masiku ano, nafenso tili ndi mwayi waukulu chifukwa ndi ife tokha amene timadziwika ndi dzina la Mulungu. Timakhalanso pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa chomudziwa ndiponso kutsogoleredwa ndi Mawu ake. Mofanana ndi wolemba Salimo 147, nanunso muyenera kuti muli ndi zifukwa zambiri zonenera kuti “Tamandani Ya” komanso zolimbikitsira anthu ena kuti azichita zimenezi. w17.07 20 ¶15-16; 21 ¶18
Lachisanu, March 22
Msilikali amene ali pa nkhondo sachita nawo zamalonda zimene anthu wamba amachita, pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali.—2 Tim. 2:4.
Masiku anonso otsatira a Yesu, omwe akuphatikizapo atumiki a nthawi zonse oposa 1 miliyoni, amachita zonse zimene angathe kuti azitsatira malangizo a Paulo omwe ali pamwambawa. Iwo amayesetsa kuti asatengeke ndi otsatsa malonda kapena maganizo a m’dzikoli, m’malomwake amakumbukira mfundo yakuti: “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.” (Miy. 22:7) Satana amafuna kuti tiziwononga nthawi yathu komanso mphamvu zathu zonse pochita zamalonda. Zinthu zina zimene tingachite m’dzikoli zikhoza kuchititsa kuti tikhale ndi ngongole kwa nthawi yaitali. Mwachitsanzo, kugula nyumba yaikulu, kupita kuyunivesite, kugula galimoto yapamwamba komanso mwambo wa ukwati wapamwamba zingachititse kuti tikhale ndi ngongole yaikulu. Timasonyeza kuti ndife anzeru tikamapewa ngongole n’kumakhala ndi moyo wosalira zambiri. Tikatero timakhala ndi mpata wotumikira Mulungu m’malo mokhala kapolo wa dzikoli.—1 Tim. 6:10. w17.07 10 ¶13
Loweruka, March 23
Ndaona kuti malamulo anu onse okhudza chilichonse ndi olungama. Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.—Sal. 119:28.
Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Iye amalamulira mwachilungamo kwambiri. Iye anati: “Ine ndine Yehova, amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi. Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa.” (Yer. 9:24) Kuti achite zinthu mwachilungamo, Yehova sadalira malamulo amene anthu omwe si angwiro analemba. Iye ndi wachilungamo kale moti amadziwa yekha zoyenera kuchita ndipo ndi amene anapereka malamulo kwa anthu. Paja Baibulo limati: “Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando [wake] wachifumu.” (Sal. 89:14) Choncho sitiyenera kukayikira kuti malamulo ake, mfundo zake komanso zonse zimene amasankha ndi zachilungamo. Koma Satana, yemwe amanena kuti Yehova salamulira bwino, walephera kuthandiza kuti zinthu ziziyenda mwachilungamo m’dzikoli. w17.06 28 ¶5
Lamlungu, March 24
Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, . . . mawu anu [ndi oona].—2 Sam. 7:28.
Yehova ndi Mulungu wachoonadi. (Sal. 31:5) Iye ndi Atate wowolowa manja ndipo amathandiza anthu amene amamuopa kuti adziwe mfundo za m’Baibulo. Kuyambira nthawi imene tinayamba kuphunzira choonadi takhala tikuphunzira mfundo zofunika kwambiri kuchokera m’Baibulo, mabuku athu, misonkhano yampingo komanso ikuluikulu. Choncho mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, tili ndi mfundo zachoonadi zakale ndiponso zatsopano zomwe takhala tikuika ‘mosungiramo chuma chathu.’ (Mat. 13:52) Tikamafunafuna mfundozi ngati chuma chobisika, Yehova amatithandiza kupeza mfundo zamtengo wapatali zatsopano zomwe tingaikenso ‘mosungiramo chuma chathu.’ (Miy. 2:4-7) Koma kodi tingachite chiyani kuti tiwonjezere mfundozi? Tiyenera kukhala ndi ndandanda yabwino yophunzira komanso kufufuza zinthu m’Baibulo ndi m’mabuku athu. Izi zingatithandize kuphunzira mfundo “zatsopano” zomwe sitinkazidziwa. (Yos. 1:8, 9; Sal. 1:2, 3) Tiyenera kuyesetsa kuwonjezera mfundo zina ‘mosungiramo chuma chathu.’ w17.06 12 ¶13-14
Lolemba, March 25
Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.—Yer. 29:12.
Mnyamata wina amene tangomupatsa dzina loti Eduardo ankacheza ndi wachikulire wina dzina lake Stephen. Mnyamatayu ankaganizira mfundo ya pa 1 Akorinto 7:28 yakuti: ‘Olowa m’banja adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.’ Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi masautso amene akutchulidwa palembali ndi ati, nanga ndingadzathane nawo bwanji ndikadzalowa m’banja?” Koma asanayankhe funsoli, Stephen anauza Eduardo kuti aganizire kaye mfundo ina imene mtumwi Paulo analemba. Mfundo yake ndi yakuti Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Yehova ndi Atate wachikondi ndipo amatilimbikitsa tikakumana ndi mavuto. Muyenera kuti mwaonapo Mulungu akukuthandizani komanso kukutsogolerani ndipo nthawi zambiri mwina anachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake. Iye amatifunira zabwino ngati mmene ankachitira ndi atumiki ake akale.—Yer. 29:11. w17.06 4-5 ¶1-2
Lachiwiri, March 26
Yehova amayang’anira alendo okhala m’dziko la eni.—Sal. 146:9.
Anthu othawa kwawo amafunika kuwathandiza kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi Yehova komanso kuti maganizo awo akhazikike. Izi n’zofunika kuposa kuwathandiza kuti apeze zofunika pa moyo. (Mat. 4:4) Mwachitsanzo, akulu angawathandize powapezera mabuku achilankhulo chawo komanso abale ndi alongo amene amadziwa chilankhulocho. Anthu ambiri akathawa amasiyana ndi achibale awo, anzawo komanso mipingo yawo. Choncho amafunika kuwaganizira kuti azidziwa kuti Yehova ndiponso Akhristu anzawo amawakonda. Kupanda kutero, angayambe kugwirizana kwambiri ndi achibale kapena anthu ena akwawo omwe si Mboni. (1 Akor. 15:33) Tikamawathandiza kuti azimasuka mumpingo ndiye kuti tikugwira ntchito limodzi ndi Yehova ‘yoyang’anira alendo okhala m’dziko la eni.’ Anthu othawa kwawo mwina sangabwerere kwawo pa nthawi imene anthu owazunzawo akulamulirabe. Komanso ambiri amavutika maganizo chifukwa cha zinthu zoipa zimene anakumana nazo. Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanakumana ndi vuto lawoli ndikanafuna kuti anthu andichitire chiyani?’—Mat. 7:12. w17.05 6-7 ¶15-16
Lachitatu, March 27
Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.—Mat. 24:12.
Kukhumudwa kungachititsenso kuti chikhulupiriro chathu chifooke ndipo tingasiye kukonda Mulungu. M’dziko la Satanali, tonsefe timakumana ndi zinthu zokhumudwitsa. (1 Yoh. 5:19) Mwina panopa tikuvutika chifukwa cha ukalamba, matenda kapena mavuto azachuma. Mwinanso tikuvutika chifukwa choti timadziona ngati olephera, timadziimba mlandu pa zimene tinalakwitsa, apo ayi chifukwa choti zimene tinkayembekezera sizikuchitika. M’malo mochita zimenezi, tiyenera kuganizira kwambiri mawu olimbikitsa osonyeza kuti Yehova sangasiye kutikonda. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 136:23 limati: “Anatikumbukira pamene adani anatinyazitsa: Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amakonda atumiki ake nthawi zonse. Choncho sitiyenera kukayikira kuti amamva ‘madandaulo athu’ ndipo amatithandiza.—Sal. 116:1; 136:24-26. w17.05 18-19 ¶8
Lachinayi, March 28
Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.—Mat. 6:15.
Lemba la Agalatiya 2:11-14 limasonyeza kuti Petulo anakodwa mumsampha wa kuopa anthu. (Miy. 29:25) Ngakhale kuti iye ankadziwa kuti Yehova alibe tsankho, anachita zolakwika chifukwa choopa Akhristu achiyuda a mumpingo wa ku Yerusalemu. Koma mtumwi Paulo anadzudzula Petulo chifukwa chochita zinthu mwachinyengo. (Mac. 15:12; Agal. 2:13) Baibulo silinena kuti Petulo anasiyitsidwa udindo wake. Iye anadzichepetsa ndipo analandira malangizo amene Paulo anam’patsa. Ndipo kenako Mulungu anamugwiritsa ntchito kulemba makalata awiri omwe anakhala mbali ya Baibulo. Yesu yemwe ndi mutu wa mpingo, anapitirizabe kumugwiritsa ntchito. (Aef. 1:22) Choncho nawonso abale ndi alongo mumpingo anayenera kutsanzira Yehova ndi Yesu n’kumukhululukira Petulo. Iwo sankafunika kulola kuti zochita za Petulo ziwafooketse. w17.04 27 ¶16-18
Lachisanu, March 29
[Mulungu] anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto, kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.—2 Pet. 2:6.
Yehova anawononga mizinda iwiriyi ndipo anathetsa zoipa zonse. Zimene anachitazi ndi “chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.” Popeza Yehova anawononga anthu a makhalidwe oipa pa nthawiyo, sadzalekerera anthu amene akuchita zoipa masiku ano. N’chiyani chidzalowa m’malo zinthu zoipazi? M’dziko latsopano mudzakhala zinthu zambiri zosangalatsa. Mwachitsanzo, padzakhala ntchito yosintha dzikoli kuti likhale Paradaiso komanso yomanga nyumba zathu ndi za anzathu. Anthu ambiri amene anamwalira adzaukitsidwa ndipo tidzawaphunzitsa mfundo za Yehova komanso zimene Yehovayo wachitira anthu. (Yes. 65:21, 22; Mac. 24:15) Tsiku lililonse tizidzachita zinthu zosangalatsa komanso zolemekeza Yehova. w17.04 12 ¶11-12
Loweruka, March 30
Ine ndidzapereka kwa Yehova aliyense amene adzatuluka m’nyumba yanga.—Ower. 11:31.
N’kutheka kuti Yefita ankadziwa kuti mwina wobwera kudzamuchingamirayo akhoza kukhala mwana wake. Komabe sizinali zophweka kuti Yefita ndi mwana wake akwaniritse lonjezoli chifukwa onsewa anafunika kudzimana zinthu zina. N’chifukwa chake Yefita atangoona mwana wakeyo, “anayamba kung’amba zovala zake” ndipo anamva chisoni. Nayenso mwanayo anapita ‘kukalirira unamwali wake.’ N’chifukwa chiyani awiriwa anachita zimenezi? N’chifukwa choti Yefita anali ndi mwana mmodzi yekhayu. Ndipo izi zinasonyeza kuti tsopano mwanayu sadzakwatiwa n’kukhala ndi ana. Choncho panalibe wodzatenga dzina komanso cholowa cha banja la Yefita. Komabe Yefita sanalole kuti izi zimulepheretse kukwaniritsa lonjezo lake. Iye anati: “Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.” Nayenso mwanayo anayankha kuti: “Ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” (Ower. 11:35-39) Yefita ndi mwana wake anali anthu okhulupirika ndipo anakwaniritsa lonjezoli kwa Yehova ngakhale kuti sizinali zophweka.—Deut. 23:21, 23; Sal. 15:4. w17.04 4 ¶5-6
Lamlungu, March 31
Ndidzayembekezera moleza mtima.—Mika 7:7.
Yosefe, yemwe anali chidzukulu cha Abulahamu, anasonyezanso kuti anali ndi mtima wotha kuyembekezera. Anthu ambiri anamuchitira zopanda chilungamo. Choyamba, iye ali ndi zaka pafupifupi 17, azichimwene ake anamugulitsa kuti akhale kapolo. Kenako ananamiziridwa kuti ankafuna kugwirira mkazi wa abwana ake ndipo anatsekeredwa m’ndende. (Gen. 39:11-20; Sal. 105:17, 18) Iye ankachita chilungamo koma m’malo modalitsidwa zinkaoneka kuti akungolangidwa. Koma patapita zaka 13, zinthu zinasintha mwamsanga. Yosefe anamasulidwa m’ndende muja n’kupatsidwa udindo wokhala wachiwiri kwa mfumu ya ku Iguputo. (Gen. 41:14, 37-43; Mac. 7:9, 10) Koma kodi Yosefe anakwiya chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene zinamuchitikirazo? Kodi anasiya kukhulupirira Yehova Mulungu? Ayi. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti adikire moleza mtima? Iye ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo anazindikira kuti Yehova ali ndi mphamvu yokonza zinthu. Umboni wake ndi zimene anauza azichimwene ake. Iye anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu? Inu munali ndi cholinga chondichitira zoipa. Koma Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.” (Gen. 50:19, 20) Yosefe anazindikira kuti anachita bwino kwambiri podikira moleza mtima. w17.08 4 ¶6; 6 ¶12-13