February
Lachisanu, February 1
Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.—Gen. 6:22.
Mulungu anauza Nowa kuti agwire ntchito yomanga chingalawa yomwe anali asanaigwirepo. Choncho iye ankadalira Yehova ndipo “anachita momwemo,” kutanthauza kuti anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anapanga bwinobwino chingalawacho popanda kulakwitsa kalikonse. Nowa ankasamaliranso bwino banja lake chifukwa chakuti ankadalira nzeru zochokera kwa Mulungu. Nzeru zimenezi zinkamuthandiza kuti aphunzitse bwino ana ake komanso aziwapatsa chitsanzo chabwino ngakhale kuti moyo pa nthawiyo unali wovuta kwambiri. (Gen. 6:5) Ngati ndinu makolo, kodi mungatani kuti muzichita zonse zimene Mulungu wakulamulani? Chofunika ndi kutsatira malangizo ake. Malangizo olerera ana mungawapeze m’Mawu ake komanso m’gulu lake. Koma ana ena amasiya Yehova ngakhale kuti makolo awo anayesetsa kuwaphunzitsa bwino. Makolo a ana oterewa sayenera kudziimba mlandu chifukwa anachita zonse zimene akanatha. Chofunika n’kukhala ndi chiyembekezo choti tsiku lina mwana wolowererayo adzabwerera kwa Yehova. w18.03 30-31 ¶10-11
Loweruka, February 2
Muzicherezana popanda kudandaula.—1 Pet. 4:9.
Kodi munafunapo kuitana anthu koma n’kulephera chifukwa chodzikayikira? Ena ndi amanyazi ndipo amaopa kuti adzasowa nkhani zoti azidzacheza ndi anthuwo kapena amaganiza kuti alendowo sangasangalale. Ena si opeza bwino ndipo amaganiza kuti sangakwanitse kupatsa anthu zimene anthu ena mumpingo angawapatse. Koma chofunika si nyumba yapamwamba koma mtima wochereza komanso nyumba yaukhondo. Ngati timaitana anthu chifukwa cha chikondi, sitiyenera kudera nkhawa chilichonse. Tizikumbukira kuti nthawi zonse kusonyeza chidwi kwa alendo n’kothandiza kwambiri. (Afil. 2:4) Pafupifupi aliyense amafuna kufotokoza zimene zachitika pa moyo wake. Ndiye pocheza ndi anthu m’pamene timakhala ndi mwayi wofotokoza zimene zachitika pa moyo wathu. Mkulu winanso analemba kuti: “Ndikaitana anthu amumpingo kunyumba kwathu ndimayamba kuwadziwa bwino komanso ndimadziwa mmene anayambira choonadi.” Kusonyeza chidwi kwa anthu ena kumathandiza kuti musangalale pocheza nawo. w18.03 17 ¶15-17
Lamlungu, February 3
Nanga ukuchedweranji? Nyamuka, ubatizidwe.—Mac. 22:16.
Makolo achikhristu amafunitsitsa kuthandiza ana awo kuti azisankha zinthu mwanzeru. Mwana akazengereza kubatizidwa zingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. (Yak. 4:17) Komabe mwana asanabatizidwe makolo amafunika kutsimikizira ngati mwanayo angakwaniritsedi udindo wake wokhala Mkhristu. Oyang’anira madera ena adandaulapo kuti amakumana ndi achinyamata ena omwe makolo awo ndi a Mboni koma sanabatizidwe ngakhale kuti atsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 kapena kupitirira. Nthawi zambiri achinyamatawa amasonkhana komanso kulowa mu utumiki ndipo amangoona kuti ndi a Mboni za Yehova. Koma pa zifukwa zina amazengereza kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Kodi n’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Nthawi zina makolo ndi amene amalimbikitsa achinyamata kuti asabatizidwe msanga. w18.03 8-9 ¶1-2
Lolemba, February 4
[Mukhale] ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.—Aroma 15:5.
Kuti titsatire mapazi a Khristu, tiyenera kudziwa bwino maganizo komanso makhalidwe ake. Nthawi zonse Yesu amaganizira ubwenzi wake ndi Mulungu. Choncho tikamatsanzira Yesu timakhala kuti tikutsanziranso Yehova. N’chifukwa chake tiyenera kuyesetsa kuti tiziganiza ngati mmene Yesu amaganizira. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Ophunzira a Yesu anamuona akuchita zozizwitsa, akukamba nkhani, akuchita zinthu ndi anthu osiyanasiyana komanso akutsatira mfundo za Mulungu. (Mac. 10:39) Koma ifeyo sitingamuone Yesu mwachindunji. Koma Yehova watipatsa nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zomwe zingatithandize kumvetsa makhalidwe a Yesu. Tikamawerenga komanso kusinkhasinkha mabuku a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane timazindikira maganizo a Khristu. Zimenezi zimatithandiza kuti ‘titsatire mapazi ake mosamala kwambiri’ komanso kuti ‘tikhale ndi maganizo’ a Khristu.—1 Pet. 2:21; 4:1. w18.02 22 ¶15-16
Lachiwiri, February 5
Munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.—Aroma 10:17.
Kuyambira kalekale, anthu okhulupirika akhala akuphunzira za Mulungu m’njira zitatu izi: poona zinthu zimene Mulungu analenga, kumva kwa atumiki ena okhulupirika komanso poona madalitso amene amapeza akamatsatira mfundo zachilungamo za Mulungu. (Yes. 48:18) Nowa akayang’ana zimene Mulungu analenga ayenera kuti ankaona umboni wakuti Mulungu aliko komanso kuzindikira makhalidwe ake monga “mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu.” (Aroma 1:20) Chifukwa cha zimenezi, Nowa sanangovomereza kuti kuli Mulungu koma anayamba kumukhulupirira ndi mtima wonse. Nowa ayenera kuti anamva kuchokera kwa achibale ake. Achibalewo anali anthu monga Lameki, yemwe anali munthu wokhulupirika ndipo anakhala ndi moyo Adamu asanamwalire. Panalinso agogo a Nowa dzina lawo Metusela ndiponso agogo a agogo ake dzina lawo Yaledi, omwe anakhala ndi moyo zaka zina 366 Nowa atabadwa. (Luka 3:36, 37) Mulimonse mmene zinalili, zimene Nowa anaphunzira zinamufika pamtima ndipo anayamba kutumikira Mulungu.—Gen. 6:9. w18.02 9 ¶4-5
Lachitatu, February 6
Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.—Aef. 4:26.
Mkhristu mnzathu kapena wachibale wathu akachita zinthu zotikhumudwitsa, zimatipweteka kwambiri. Ndiye kodi tingatani ngati zikutivuta kuiwala nkhaniyo? Kodi tidzapitiriza kumusungira chakukhosi kwa zaka zambiri? Kapena kodi tidzatsatira malangizo anzeru a m’Baibulo akuti tizithetsa nkhani mwamsanga? Tikachedwa kwambiri kuthetsa nkhani m’pamene nkhaniyonso imavuta kwambiri kuithetsa. Kodi mungatani kuti muyambenso kugwirizana? Choyamba, muyenera kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukambirana bwinobwino ndi m’baleyo. Muzikumbukira kuti nayenso ndi mnzake wa Yehova. (Sal. 25:14) Mulungu amakomera mtima anzake ndipo amafuna kuti nafenso tizichita zomwezo. (Miy. 15:23; Mat. 7:12; Akol. 4:6) Kenako muyenera kuganizira mofatsa zimene mungakalankhule. Musamafulumire kuganiza kuti wakukhumudwitsani dala. Muyeneranso kuzindikira kuti mwina inunso munachita zinazake zimene zinachititsa kuti musemphane. w18.01 10 ¶15-16
Lachinayi, February 7
Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana.—Yoh. 13:34.
Mosiyana ndi anthu amene sakonda anzawo masiku ano, anthu amene amalambira Yehova amasonyeza anzawo chikondi ndipo sichikhala champeni kumphasa. Anthu a Yehova akhala akuchita zimenezi kuyambira kalekale. Tikutero chifukwa Yesu atanena kuti lamulo lalikulu m’Chilamulo cha Mose ndi kukonda Mulungu, ananena kuti lachiwiri lake ndi kukonda anzathu. (Mat. 22:38, 39) Iye ananenanso kuti kukondana ndi khalidwe limene Akhristu oona ayenera kudziwika nalo. (Yoh. 13:35) Akhristu amasonyezanso chikondi ngakhale kwa adani awo. (Mat. 5:43, 44) Yesu ankasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu. Iye ankayenda kumzinda ndi mzinda kukauza anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ankachiritsa anthu osaona, olumala, akhate, osamva ndiponso kuukitsa akufa. (Luka 7:22) Yesu anafikanso popereka moyo wake kuti awombole anthu. Yesu ankatsanzira Atate wake ndendende posonyeza chikondi. Padziko lonse, a Mboni za Yehova amasonyezanso chikondi chenicheni kwa anthu anzawo. w18.01 29-30 ¶11-12
Lachisanu, February 8
Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.—Afil. 4:13.
Mwina munabatizidwa muli wamng’ono ndipo simungadziwe mayesero amene mungakumane nawo m’tsogolo. Kukumbukira kuti simungasinthe zimene munalonjeza podzipereka kwa Yehova kungakuthandizeni kukhalabe wokhulupirika. Paja munalonjeza Wolamulira chilengedwe chonse kuti mudzamutumikirabe ngakhale makolo kapena anzanu atasiya kumutumikira. (Sal. 27:10) Yehova angakuthandizeni nthawi zonse kukhala ndi mphamvu zoti muzikwaniritsa zimene munalonjezazo. (Afil. 4:11, 12) Yehova amafuna kuti mukhale mnzake. Koma muyenera kuchita khama kuti mukhalebe pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti mudzapulumuke. N’chifukwa chake lemba la Afilipi 2:12 limati: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.” Choncho muyenera kuganizira zimene zingakuthandizeni kukhala wokhulupirika kwa Yehova zivute zitani. Si bwino kudzidalira pa nkhani imeneyi chifukwa ngakhale anthu amene akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali amasokonezeka. w17.12 24 ¶4, 6-7
Loweruka, February 9
Ndapereka zinthu zonsezi mwaufulu.—1 Mbiri 29:17.
Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wothandiza pa ntchito yaikulu imene gulu lake likugwira masiku ano. Iye walonjeza kuti anthu amene amapereka zinthu zawo kuti zithandize pa ntchito za Ufumu adzadalitsidwa. (Mal. 3:10) Yehova ananeneratu kuti munthu amene amapereka mowolowa manja, zinthu zidzamuyendera bwino. (Miy. 11:24, 25.) Munthu wopatsa amasangalalanso kwambiri chifukwa Baibulo limanena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Choncho zolankhula komanso zochita zathu ziyenera kuthandiza ana athu komanso anthu atsopano kuzindikira zimene angachite kuti azipereka kwa Yehova ndiponso madalitso amene angalandire. Chilichonse chimene tili nacho n’chochokera kwa Yehova. Choncho tikamamupatsa zinthu zimenezi timasonyeza kuti timamukonda komanso timayamikira zimene amatichitira. Baibulo limanena kuti anthu amene anapereka zinthu zothandiza pomanga kachisi “anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, pakuti anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 29:9) Tiyeni nafenso tizipereka zinthu zimene Yehova watipatsa ndipo tikamatero tidzakhala osangalala kwambiri. w18.01 21 ¶18-19
Lamlungu, February 10
Aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.—1 Akor. 15:23.
Kuuka koyamba kunayenera kuchitika pambuyo poti nthawi ya “kukhalapo” kwa Khristu yayamba. Odzozedwa amene adzakhalebe moyo pa nthawi ya chisautso chachikulu ‘adzatengedwa m’mitambo.’ (1 Ates. 4:13-17; Mat. 24:31) Iwo ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza.’ (1 Akor. 15:51, 52) Masiku ano, Akhristu ambiri si odzozedwa ndipo sanaitanidwe kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. M’malomwake akuyembekezera “tsiku la Yehova” pamene dziko loipali lidzawonongedwa. Palibe amene akudziwa deti limene tsikuli lidzafike koma pali umboni wotsimikizira kuti layandikira kwambiri. (1 Ates. 5:1-3) Pambuyo pa tsikuli, anthu ena adzaukitsidwa kuti akhale m’paradaiso padziko lapansi. Anthu amene adzaukewo adzakhala ndi mwayi wothandizidwa kuti akhale angwiro komanso apatsidwe moyo wosatha. w17.12 11 ¶15; 12 ¶18-19
Lolemba, February 11
Pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano, palinso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.—Yak. 3:16.
Tikamayesetsa kukhala achikondi ndiponso okoma mtima, sitidzachitira ena nsanje. Paja Baibulo limati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje.” (1 Akor. 13:4) Kuti tisamachite nsanje tiyenera kuyesetsa kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Tiyenera kuona kuti ndife thupi limodzi ndi abale ndi alongo athu. Maganizo amenewa angatithandize kuti tizikondana mogwirizana ndi malangizo akuti: “Chiwalo chimodzi chikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalira nacho limodzi.” (1 Akor. 12:16-18, 26) Choncho m’malo mochita nsanje mnzathu akadalitsidwa, tiyenera kusangalala naye. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mwana wa Mfumu Sauli dzina lake Yonatani. M’malo mochitira nsanje Davide atasankhidwa kuti alowe ufumu wa Sauli, anamulimbikitsa. (1 Sam. 23:16-18) Nafenso tiyenera kuyesetsa kukhala achikondi komanso okoma mtima ngati Yonatani. w17.11 27 ¶10-11
Lachiwiri, February 12
Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima.—Yes. 11:3, 4.
Yehova anaonetsetsa kuti Chilamulo chikhale m’Baibulo kuti tizichiwerenga. Iye safuna kuti tiziganizira kwambiri tinthu ting’onoting’ono ta m’Chilamulo koma tiziganizira “zinthu zofunika” zomwe ndi mfundo zake zikuluzikulu. (Mat. 23:23) Chilamulo cha Mose chinkathandiza anthu kudziwa choonadi pa nkhani ya Yehova ndiponso mfundo zake zachilungamo. (Aroma 2:20) Mwachitsanzo, nkhani ya mizinda yothawirako imathandiza akulu kuti azichita “chilungamo chenicheni poweruza milandu.” Imatiphunzitsanso tonsefe kuti tiyenera kusonyezana “kukoma mtima kosatha ndi chifundo.” (Zek. 7:9) N’zoona kuti masiku ano sitiyendera Chilamulo cha Mose. Koma Yehova sasintha, choncho amaonabe kuti chilungamo ndi chifundo ndi makhalidwe ofunika kwambiri. Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kulambira Mulungu amene anatilenga m’chifaniziro chake, amene tikhoza kumutsanzira komanso amene tikhoza kuthawira kwa iye. w17.11 13-14 ¶2-3; 17 ¶18-19
Lachitatu, February 13
Wodala ndi munthu amene wapeza nzeru, ndiponso munthu amene wapeza kuzindikira.—Miy. 3:13.
Abale amene amaphunzitsa pamisonkhano ayenera kuonetsetsa kuti akugwiritsa ntchito bwino Malemba pokamba nkhani yawo. (Yoh. 7:16) Kodi mungachite bwanji zimenezi? Choyamba, muziyesetsa kuti anthu aziganizira kwambiri malemba amene mukugwiritsa ntchito m’malo moganizira kwambiri zitsanzo zanu, mafanizo kapenanso kalankhulidwe kanu. Muzikumbukiranso kuti kungowerenga malemba sikutanthauza kuti mukugwiritsa ntchito bwino malembawo pophunzitsa. Komanso kugwiritsa ntchito malemba ambiri kungachititse kuti anthu asawakumbukire. Choncho muyenera kusankha bwino malemba anu n’cholinga choti muthe kuwawerenga, kuwafotokoza, kupereka fanizo komanso kusonyeza mmene malembawo angathandizire anthu. (Neh. 8:8) Ngati nkhani imene mukufuna kukamba ndi yochokera mu autilaini yokonzedwa ndi gulu, muyenera kuikonzekera bwino n’kuona malemba onse. Yesetsani kuti muone kugwirizana pakati pa mfundo za pa autilaini ndi malemba ake. Koma chofunika kwambiri ndi kupempha Yehova kuti akuthandizeni kufotokoza bwino mfundo zofunika za m’Mawu ake.—Ezara 7:10. w17.09 26 ¶11-12
Lachinayi, February 14
Bwererani kwa ine, . . . ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.—Zek. 1:3.
M’chaka cha 537 B.C.E. anthu a Yehova anasangalala kwambiri chifukwa anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo komwe anakhalako zaka 70. Iwo anasangalala kubwerera ku Yerusalemu kuti akamangenso kachisi n’kumalambira Yehova. Maziko a kachisiyu anamangidwa mu 536 B.C.E. Koma patapita zaka 16, ntchito yomanga kachisi wa Yehova inali itaimiratu. Anthu a Mulungu anafunika kukumbutsidwa kuti abwerere kwa Yehova m’malo moika patsogolo zochita zawo. Choncho mu 520 B.C.E., Yehova anatuma mneneri Zekariya kuti akumbutse Aisiraeliwo chifukwa chimene anawamasulira ku ukapolo wa ku Babulo. Ndipotu n’kutheka kuti dzina loti Zekariya, lomwe limatanthauza kuti “Yehova Wakumbukira,” linawakumbutsa za mfundo ina yofunika. Mfundo yake ndi yakuti ngakhale kuti Aisiraeli anaiwala zimene Yehova anawachitira, Mulungu ankawakumbukirabe. (Zek. 1:3, 4) Iye anawatsimikizira kuti adzawathandiza kuti ayambirenso kumulambira moyenera, koma anawachenjeza kuti sadzalekerera anthu amene samulambira ndi mtima wonse. w17.10 21-22 ¶2-3
Lachisanu, February 15
Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu.—Aef. 4:32.
Akatswiri azamaganizo amanena kuti kusonyeza chifundo kumathandiza munthu kukhala wathanzi, wosangalala komanso kuti azigwirizana ndi anzake. Munthu akathandiza anzake amamva bwino mumtima, nkhawa zake zimachepa ndipo saganizira kwambiri zinthu zokhumudwitsa. Zonsezi zikusonyeza kuti kuchitira ena chifundo kumatithandizanso ifeyo. Akhristu amene amathandiza anthu ena amakhala ndi chikumbumtima chabwino chifukwa chodziwa kuti akutsatira mfundo za makhalidwe abwino. Mtima wachifundo umathandiza munthu kukhala wabwino kwa ana ake, mwamuna kapena mkazi wake komanso kwa anzake. Ndipo anthu amene amakonda kuthandiza anzawo nawonso akhoza kuthandizidwa akakumana ndi vuto. (Mat. 5:7; Luka 6:38) Koma sikuti tizingochitira ena chifundo n’cholinga choti ifeyo tipezepo phindu. Cholinga chachikulu pochitira ena chifundo chizikhala kutsanzira Yehova Mulungu wathu wachifundo komanso kumulemekeza.—Miy. 14:31. w17.09 12 ¶16-17
Loweruka, February 16
Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.—Zek. 6:13.
Kuwonjezera pa udindo wake monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu wapatsidwa ntchito ‘yomanga kachisi wa Yehova.’ Pa ntchito yake yomangayi, Yesu wamasula anthu a Mulungu mu ukapolo wa Babulo Wamkulu ndipo anakhazikitsanso mpingo wachikhristu mu 1919. M’chaka chimenechi anasankhanso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitsogolera pa ntchito imene ikugwiridwa pabwalo la padziko lapansi la kachisi wamkulu wauzimu. (Mat. 24:45) Yesu wakhala akugwiranso ntchito yoyeretsa anthu a Mulungu powathandiza kuti azilambira Mulungu m’njira yoyenera. (Mal. 3:1-3) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu ndi anthu 144,000, amenenso ndi mafumu ndi ansembe, adzathandiza anthu okhulupirika kuti akhale angwiro. Zimenezi zikadzachitika, padzikoli padzatsala anthu olambira Yehova okhaokha ndipo kulambira koyera kudzakhala kutabwezeretsedwa padziko lonse. w17.10 29 ¶15-16
Lamlungu, February 17
Iye ayenera kukhala [mumzinda wothawirako] mpaka mkulu wa ansembe . . . adzamwalire.—Num. 35:25.
Munthu amene wapha mnzake mwangozi ankayenera kuchitapo kanthu kuti achitiridwe chifundo. Iye ankayenera kuthawira kumzinda wothawirako wapafupi. (Yos. 20:4) Wopha mnzake mwangozi ayenera kuti sankanyalanyaza zimenezi chifukwa popanda kuthawira kumzindawu akanatha kuphedwa. Koma panali zinthu zina zimene ankayenera kudzimana kuti apulumuke. Ankayenera kusiya ntchito yake, nyumba yake komanso ufulu wopita kumene akufuna chifukwa ankayenera kukhala mumzindawu mpaka mkulu wa ansembe atafa. Koma ankalolera kusiya zonsezi n’cholinga choti asaphedwe. Masiku anonso anthu amene achita tchimo lalikulu ndipo alapa ayeneranso kuchitapo kanthu kuti Mulungu awachitire chifundo. Ayenera kusiyiratu tchimolo komanso kupewa zinthu zimene zingawachititse kuti achite machimo ena akuluakulu. Tikachita zinthu mwamsanga kuti tikonze zimene talakwitsa, Yehova amaona kuti sitikuona nkhaniyo mopepuka komanso sitichita dala machimo poganiza kuti atichitira chifundo. 2 Akor. 7:10-11. w17.11 10-11 ¶10-11
Lolemba, February 18
Muzicherezana popanda kudandaula.—1 Pet. 4:9.
Yehova amatiuza kuti tiyenera kuthandiza abale ndi alongo athu. (1 Yoh. 3:17) Koma tiyenera kuchita zimenezi ndi zolinga zabwino osati pofuna kupindulapo kenakake. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nthawi zambiri ndimangochereza anzanga apamtima, anthu otchuka kapena amene akhoza kudzandicherezanso? Kapena kodi ndimayesetsa kucherezanso abale ndi alongo amene sindikuwadziwa bwino kapena amene sangakwanitse n’komwe kundicherezanso?’ (Luka 14:12-14) Nanga bwanji ngati Mkhristu mnzathu akufunikira thandizo chifukwa chochita zinthu mosaganiza bwino kapena ngati sanatithokoze pamene tinamuthandiza? Zikatero, tiyenera kutsatira malangizo amulemba la lero. Mukamatsatira malangizowa mudzakhala osangalala kwambiri chifukwa chothandiza anthu muli ndi zolinga zabwino.—Mac. 20:35. w17.10 9-10 ¶12
Lachiwiri, February 19
Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?—Gen. 39:9.
Mkazi wa Potifara anayamba kukopa Yosefe chifukwa iye anali “wokongola m’maonekedwe ndi wa thupi loumbika bwino.” Koma Yosefe sanalole kugona naye. Ndipo zitafika povuta. Yosefe anathawa. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yosefe? Tikuphunzira kuti nthawi zina tiyenera kuthawa zinthu zina n’cholinga choti tisaphwanye lamulo la Mulungu. (Miy. 1:10) Anthu ena asanakhale a Mboni ankachita zinthu monga kudya mopitirira malire, kuledzera, kusuta, kumwa mankhwala osokoneza bongo komanso chiwerewere. Ngakhale atabatizidwa mwina ankavutika kuti asayambirenso kuchita zimenezi. Koma mukamayesedwa kuti muphwanye lamulo la Mulungu muyenera kuganizira mavuto amene angabwere chifukwa cholephera kudziletsa. Muyenera kuganiziranso zimene zingakubweretsereni mayesero n’kuoneratu mmene mungapewere zinthuzo. (Sal. 26:4, 5; Miy. 22:3) Ndiyeno mayeserowo akafika, muzipempha Yehova kuti akupatseni nzeru komanso akuthandizeni kukhala odziletsa. w17.09 4-5 ¶8-9
Lachitatu, February 20
Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama, kuti chumacho chikatha, akakulandireni m’malo okhala amuyaya.—Luka 16:9.
Njira ina yothandizira kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova ndi kufunafuna “chuma chenicheni” m’malo mochita kwambiri zamalonda. Abulahamu, yemwe anali ndi chikhulupiriro cholimba, anamvera Yehova ndipo anachoka mumzinda wotukuka wa Uri n’kumakakhala m’mahema. Iye sanasiye kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. (Aheb. 11:8-10) Nthawi zonse ankadalira Mulungu podziwa kuti amapereka “chuma chenicheni.” Ankapewanso kuchita chilichonse chosonyeza kuti ankadalira chuma osati Mulungu. (Gen. 14:22, 23) Yesu ankalimbikitsa anthu kuti akhale ndi chikhulupiriro choterechi pamene anauza mnyamata wina wachuma kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Mat. 19:21) Zikuoneka kuti mnyamatayo analibe chikhulupiriro ngati cha Abulahamu, komabe pali anthu ena amene amakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse. w17.07 10 ¶12
Lachinayi, February 21
[Yehova] anamulonjeza kuti adzamupatsa [Abulahamu] dzikoli monga cholowa chake, ndi cha mbewu yake, ngakhale kuti pa nthawiyo n’kuti alibe mwana.—Mac. 7:5.
Panadutsa zaka 430 kuchokera nthawi imene Abulahamu anawoloka mtsinje wa Firate kufika nthawi imene ana ake anakhala mtundu waukulu n’kulandira dziko lolonjezedwalo. (Eks. 12:40-42; Agal. 3:17) Abulahamu anatha kudikira moleza mtima chifukwa choti ankakhulupirira Yehova. (Aheb. 11:8-12) Iye anadikira moyo wake wonse koma sanaone lonjezo lonse litakwaniritsidwa. Ngakhale zinali choncho, sanadandaule. Koma tangoganizirani mmene adzamvere akadzaukitsidwa padzikoli. Iye adzadabwa kuona kuti m’Baibulo muli mavesi ambiri ofotokoza za iye ndi ana ake. Adzasangalalanso kudziwa kuti zimene anachita zinali zofunika kwambiri kuti cholinga cha Yehova chokhudza mbewu yolonjezedwa chikwaniritsidwe. Mosakayikira, adzaona kuti anachita bwino kwambiri kudikira moleza mtima. w17.08 5-6 ¶10-11
Lachisanu, February 22
Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku . . . zinthu zodetsa.—Akol. 3:5.
Mawu a m’Baibulo amene anawamasulira kuti “zinthu zodetsa” amatanthauza zambiri osati zokhudza kugonana basi. Akhoza kutanthauza zinthu monga kusuta kapena nthabwala zotukwana. (2 Akor. 7:1; Aef. 5:3, 4) Angatanthauzenso zinthu zimene munthu angachite ali kwayekha monga kuwerenga mabuku onena zachiwerewere kapena kuonera zolaula ndipo zimenezi zingamuchititse kuti ayambe khalidwe lodetsa la kuseweretsa maliseche. Anthu amene amakonda kuonera zolaula amakhala ndi “chilakolako cha kugonana” champhamvu moti sangathe kudziletsa ndipo izi zingachititse kuti akhale achiwerewere. Ochita kafukufuku anapeza kuti anthu amene amakonda kuonera zolaula zimawavuta kusiya ngati mmene zimakhalira ndi zidakwa kapena anthu omwe amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. M’pake kuti anthu amene amaonera zolaula nthawi zambiri amadziimba mlandu, sagwira bwino ntchito, amakhala ndi mavuto a m’banja komanso nthawi zina amadzipha. w17.08 19 ¶8-9
Loweruka, February 23
Walimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Wadalitsa ana ako amene ali mwa iwe. Iye akukhazikitsa mtendere m’dziko lako.—Sal. 147:13, 14.
Poganizira zimene zinachitika Ayuda atabwerera ku Yerusalemu, wolemba salimo ananena mawu ali pamwambawa okhudza Yehova. Wolemba salimoyu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti Mulungu adzalimbitsa mageti n’cholinga choti anthu amene amamulambira akhale otetezeka. Mwina mungakumane ndi mavuto amene angakudetseni nkhawa kwambiri. Koma Yehova angakupatseni nzeru zokuthandizani kuthana ndi mavutowo. Wolemba salimoyo ananena kuti Mulungu “amatumiza mawu ake padziko lapansi, ndipo mawu akewo amathamanga kwambiri.” Iye ananenanso kuti Yehova ‘amapereka chipale chofewa, amamwaza mame oundana komanso amaponya madzi oundana.’ Kenako anafunsa kuti: “Ndani angaime m’chisanu chake?” Iye ananenanso kuti Yehova “amatumiza mawu ake ndi kusungunula madzi oundanawo.” (Sal. 147:15-18) Mulungu wathu ndi wanzeru kwambiri, wamphamvu zonse komanso akhoza kuletsa matalala kapena chipale chofewa kuti zisagwe. Choncho akhozanso kukuthandizani kuthana ndi vuto lililonse limene mungakumane nalo. w17.07 20 ¶14-15
Lamlungu, February 24
Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse.—Chiv. 4:11.
Ulamuliro wa Mulungu ndi woyenera komanso wabwino kwambiri. Tonsefe tiyenera kukhala kumbali ya ulamuliro umenewu. Iye ndi woyenera kulamulira anthu komanso angelo. Satana sanalenge chinthu ngakhale chimodzi. Chifukwa cha zimenezi si woyenera kulamulira. Iye limodzi ndi Adamu ndi Hava anachita zinthu modzikuza kwambiri pogalukira ulamuliro wa Yehova. (Yer. 10:23) N’zoona kuti anali ndi ufulu wosankha zochita. Koma kodi anagwiritsa ntchito ufuluwu moyenera? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti anthu ali ndi ufulu wosankha zochita za tsiku ndi tsiku koma alibe ufulu wogalukira Mulungu amene anawalenga. Choncho anthufe tiyenera kugonjera ulamuliro wa Yehova womwe ndi wachilungamo. w17.06 27-28 ¶2-4
Lolemba, February 25
Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki.—Mac. 20:24.
Ngati timakonda kwambiri utumiki wathu, tidzatsanzira Paulo n’kumalalikira ngakhale pamene tikutsutsidwa. (Mac. 14:19-22) Cha m’ma 1930 ndi m’ma 1940, abale athu ku United States ankatsutsidwa kwambiri. Koma mofanana ndi Paulo, sanasiye kulalikira ndipo anayesetsa kumenyera ufulu wochitira zimenezi m’makhoti. Mu 1943, M’bale Nathan H. Knorr anafotokoza za mlandu wina umene tinawina kukhoti lalikulu kwambiri la ku United States kuti: “Timawina milandu chifukwa cha khama lanu. Abale akanasiya kulalikira si bwenzi kukhoti lalikululi kuli milandu. Koma chifukwa choti abale ndi alongo inu mukulalikirabe mwakhama padziko lonse ndipo simungasiye, tikutha kugonjetsa anthu amene akutizunza. Kusagonja kwa anthu a Mulungu kumeneku n’komwe kwathandiza kuti mlanduwu tiuwine.” Zinthu ngati zimenezi zachitikanso m’mayiko osiyanasiyana. Apa zikuonekeratu kuti kukonda utumiki kumathandiza kuti tigonjetse anthu amene amatizunza. Ngati timaona kuti utumiki ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova, sitilalikira n’cholinga choti tingopeza maola. M’malomwake, timachita chilichonse chimene tingathe kuti ‘tichitire umboni mokwanira za uthenga wabwino.’—2 Tim. 4:5. w17.06 11-12 ¶11-12
Lachiwiri, February 26
Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.—Mat. 22:37.
Kukonda kwambiri Yehova kungatichititse kuti tizikonda malamulo ake, tikhale opirira ndiponso kuti tizidana ndi zinthu zoipa. (Sal. 97:10) Komabe, dziko loipali ndiponso zochita za Satana zikhoza kutichititsa kuti tisiye kukonda Mulungu. Anthu a m’dzikoli amakonda zinthu zolakwika. M’malo mokonda Mlengi wawo, ‘amadzikonda’ okha. (2 Tim. 3:2) Dziko lolamulidwa ndi Satanali limalimbikitsa “chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake za kuopsa komangochita zimene thupi lawo likufuna. Iye anati: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa . . . chifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani ndi Mulungu.” (Aroma 8:6, 7) Ndipotu anthu amene moyo wawo wonse amangokhalira kufunafuna chuma kapena kuchita dama, pa mapeto pake amaona kuti sanapindule chilichonse ndipo amakhumudwa.—1 Akor. 6:18; 1 Tim. 6:9, 10. w17.05 18 ¶5-6
Lachitatu, February 27
Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.—2 Ates. 3:10.
Abale amene athawa kwawo akamayamikira zimene ena akuwachitira ndiponso kupewa kupempha zinthu zambiri, abale amene akuwathandizawo amasangalala kwambiri. Koma si bwino kuti anthu othawa kwawo azingodalira kuthandizidwa ndi Akhristu anzawo. Zimenezi zingawachotsere ulemu komanso zingachititse kuti asiye kugwirizana ndi abale ena. (2 Ates. 3:7-9) Ngakhale zili choncho, timafunikabe kuwathandiza. Koma sikuti pamafunika ndalama zambiri kuti tichite zimenezi. Chimene chimafunika ndi kupeza nthawi yowathandiza ndiponso kuwasonyeza chikondi. Nthawi zina tingafunike kuwathandiza kudziwa mmene angamayendere popita kumalo osiyanasiyana komanso mmene angagulire zakudya zabwino pamtengo wotsika. Mwinanso tingawathandize kupeza zipangizo zomwe angamagwiritse ntchito kuti azipeza kangachepe. Chofunika kwambiri n’kuwathandiza kuti asamachite chilendo mumpingo. Mwina tingawathandize pa nkhani ya kayendedwe popita kumisonkhano. Tingawatengenso polowa mu utumiki n’kumawafotokozera zimene anganene polalikira anthu m’gawolo. w17.05 5-6 ¶11-12
Lachinayi, February 28
Muzilakalaka mkaka wosasukuluka umene uli m’mawu a Mulungu, kuti mwa kumwa mkakawo, mukule ndi kukhala oyenera chipulumutso.—1 Pet. 2:2.
Anthu amene amakonda zinthu za m’dzikoli amavutika kuti azikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma. (1 Akor. 2:14) Popeza kuti saganiza bwino, zimawavuta kuti asiyanitse choyenera ndi chosayenera. (Aheb. 5:11-14) N’chifukwa chake amangokhalira kufunafuna chuma ndipo sakhutira. (Mlal. 5:10) Komabe tikhoza kupewa zimenezi tikamawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. Yesu anatha kukana mayesero chifukwa choganizira Mawu a Mulungu. Nafenso tikamatsatira mfundo za m’Baibulo tikhoza kupewa mtima wokonda chuma. (Mat. 4:8-10) Tikamachita zimenezi, Yesu amaona kuti timamukonda kwambiri kuposa chuma. w17.05 26 ¶17