Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 7-17
  • January

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Lachiwiri, January 1
  • Lachitatu, January 2
  • Lachinayi, January 3
  • Lachisanu, January 4
  • Loweruka, January 5
  • Lamlungu, January 6
  • Lolemba, January 7
  • Lachiwiri, January 8
  • Lachitatu, January 9
  • Lachinayi, January 10
  • Lachisanu, January 11
  • Loweruka, January 12
  • Lamlungu, January 13
  • Lolemba, January 14
  • Lachiwiri, January 15
  • Lachitatu, January 16
  • Lachinayi, January 17
  • Lachisanu, January 18
  • Loweruka, January 19
  • Lamlungu, January 20
  • Lolemba, January 21
  • Lachiwiri, January 22
  • Lachitatu, January 23
  • Lachinayi, January 24
  • Lachisanu, January 25
  • Loweruka, January 26
  • Lamlungu, January 27
  • Lolemba, January 28
  • Lachiwiri, January 29
  • Lachitatu, January 30
  • Lachinayi, January 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 7-17

January

Lachiwiri, January 1

Anthu okonda kuchita zoipa sangamvetse chilungamo.​—Miy. 28:5.

Pamene mapeto akuyandikira, anthu oipa ‘akuphuka ngati msipu.’ (Sal. 92:7) Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri alibe makhalidwe abwino. Ndiyeno kodi ifeyo tingatani kuti tikhale “tiana pa zoipa” koma ‘aakulu msinkhu pa luntha la kuzindikira’? (1 Akor. 14:20) Yankho la funsoli tingalipeze mulemba lathu la tsiku lomwe likuti: “Amene akufunafuna Yehova amamvetsa chilichonse.” Palembali, mawu akuti “chilichonse” akutanthauza chilichonse chofunika kuti tizisangalatsa Mulungu. Mfundo yofanana ndi imeneyi ikupezekanso pa Miyambo 2:7, 9, pamene pamanena kuti Yehova ‘amasungira anthu owongoka mtima nzeru zopindulitsa.’ Izi zimawathandiza kuti azimvetsa “zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.” Nowa, Danieli ndi Yobu anapeza nzeru zimenezi. (Ezek. 14:14) N’chimodzimodzinso ndi anthu a Mulungu masiku ano. Koma bwanji za inuyo panokha? Kodi ‘mumamvetsa chilichonse’ chofunika kuti musangalatse Yehova? Kuti muthe kuchita zimenezi, muyenera kumudziwa bwino Yehova. w18.02 8 ¶1-3

Lachitatu, January 2

Anabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.​—Mac. 19:5.

Munthu sayenera kukakamizidwa ndi makolo, anthu amene akuphunzira nawo Baibulo kapena aliyense mumpingo kuti abatizidwe. Yehova safuna kuti munthu azimumvera chifukwa chokakamizika. (1 Yoh. 4:8) Choncho tikamaphunzitsa anthu, tiyenera kuwathandiza kuona kuti kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu n’kofunika kwambiri. Wophunzira angafune kubatizidwa akayamba kukonda kwambiri choonadi komanso kufunitsitsa kukhala wotsatira wa Khristu. (2 Akor. 5:14, 15) Sikuti munthu amayenera kubatizidwa akafika pa msinkhu winawake. Ophunzira Baibulo amaphunzira komanso kusintha mosiyanasiyana. Tsiku la ubatizo limakhala losangalatsa kwambiri. Koma imakhalanso nthawi yakuti munthu aziganizira kwambiri kufunika kwa zimene wasankhazo. Munthu amafunika kuchita khama kuti azichita zimene analonjeza kwa Yehova. N’chifukwa chake Yesu anayerekezera udindo wokhala Mkhristu ndi goli. Otsatira a Yesu sayenera ‘kukhala moyo wongodzisangalatsa okha, koma wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.’​—2 Akor. 5:15; Mat. 16:24. w18.03 6-7 ¶14-17

Lachinayi, January 3

Musaiwale kuchereza alendo, pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.​—Aheb. 13:2.

Kodi munakayikirapo kuitana anthu pa zifukwa zina? Ngati zili choncho, mwinatu munaphonya mwayi wocheza ndi anthu ena komanso kupeza anzanu abwino kwambiri. Kuchereza alendo ndi kumene kungathandize munthu kuti asamasowe ocheza nawo. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani munthu angakayikire kuitana anthu?’ Pangakhale zifukwa zingapo. Chifukwa chimodzi chingakhale chakuti atumiki a Yehova amakhala ndi zochita zambiri. Choncho ena amaona kuti alibe nthawi komanso atopa moti sangachereze alendo. Ngati ndi mmene zilili ndi inuyo, mwina mungachite bwino kuonanso zimene mumachita tsiku lililonse. Kodi mungasinthe zinthu zina n’cholinga choti mukhale ndi nthawi yoitanira anthu kapena yopita kukacheza ndi anthu ena? Malemba amalimbikitsa Akhristu kuti azikhala ochereza. Si kulakwa kupeza nthawi yochitira zimenezi, ndipotu ndi zimene tiyenera kuchita. Koma muyenera kukhala okonzeka kusintha zinthu zina zimene mumachita. w18.03 16 ¶13-14

Lachisanu, January 4

Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.​—Luka 4:43.

Pa anthu onse amene anakhalapo, kodi ndi ndani amene anapereka chitsanzo chabwino kwambiri chokhala munthu wauzimu? Palibenso wina koma Yesu. Pa moyo wake komanso utumiki wake anasonyeza kuti ankafunitsitsa kutsanzira Atate wake Yehova. Iye ankatsanzira maganizo komanso mtima wa Yehova. Zonse zimene ankachita zinali zogwirizana ndi cholinga cha Mulungu komanso mfundo zake. (Yoh. 8:29; 14:9; 15:10) Mwachitsanzo, tayerekezerani zimene Yesaya analemba zokhudza chifundo cha Yehova ndi zimene Maliko analemba zokhudza chifundo cha Yesu. (Yes. 63:9; Maliko 6:34) Kodi ifeyo timatsanzira Yesu n’kumakhala okonzeka kuthandiza anthu ovutika? Yesu ankachitanso khama kwambiri pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. Zonse zimene Yesu ankachitazi zimasonyeza kuti ndi wauzimu. w18.02 21 ¶12

Loweruka, January 5

[Muzilera ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.​—Aef. 6:4.

Kulera ana masiku ano si kophweka. (2 Tim. 3:1-5) Ana sabadwa ndi mtima wotha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika. Iwo amangobadwa ndi chikumbumtima ndipo chimafunika kuphunzitsidwa bwino kuti akhale odziletsa. (Aroma 2:14, 15) Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti mawu amene anamasuliridwa kuti “malangizo” angamasuliridwenso kuti “zothandiza mwana kukula.” Ana amene amapatsidwa malangizo oyenera amaona kuti ndi otetezeka. Amadziwa kuti ufulu wawo uli ndi malire ndipo zimene amachita zingakhale ndi zotsatirapo zake, zabwino kapena zoipa. Choncho ndi bwino kuti makolo achikhristu azidalira malangizo a Yehova. Chinthu china chofunika kuchikumbukira n’chakuti maganizo a anthu komanso njira zolerera ana zimakhala zosiyana malinga ndi chikhalidwe komanso zimasintha pakapita nthawi. Koma malangizo a Yehova amathandiza kuti makolo azidziwa zochita polera ana ndipo sadalira nzeru za anthu. w18.03 30 ¶8-9

Lamlungu, January 6

Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.​—Afil. 2:12.

Popeza kuti munabatizidwa, panokha muli ndi udindo wolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Choncho ngakhale kuti mukukhalabe ndi makolo anu, udindo wochita zinthu zokuthandizani kudzapulumuka ndi wanu. Muyenera kukumbukira mfundoyi chifukwa chakuti pamene mukukula mukhoza kuyamba kulakalaka zinthu zina komanso kukumana ndi mayesero osiyanasiyana. Pa nkhaniyi, mtsikana wina anati: “Kamwana sikangaganize kuti kukhala wa Mboni za Yehova n’koipa chifukwa choti kakumanidwa keke imene ana anzake akudya pa tsiku lawo lobadwa. Koma akamakula n’kuyamba kulakalaka kugonana, amafunika kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu chomuthandiza kukumbukira kuti kutsatira malamulo a Yehova n’kothandiza nthawi zonse.” Ngakhale anthu amene anabatizidwa atakula kale amakumananso ndi mayesero amene sankawayembekezera. Akhoza kukumana ndi mavuto a m’banja, matenda kapena mavuto ena okhudza ntchito. Choncho munthu aliyense, kaya ndi wamkulu kapena wamng’ono, adzakumana ndi mayesero enaake ndipo adzafunika kusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova.​—Yak. 1:12-14. w17.12 24 ¶4-5

Lolemba, January 7

Kwiyani, koma musachimwe.—Aef. 4:26.

Si anthu ambiri amene akumanapo ndi mavuto aakulu ngati amene Davide anakumana nawo. Koma iye sanalole kuti azingokhala wokwiya. M’malomwake, analemba kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya. Usapse mtima kuti ungachite choipa.” (Sal. 37:8) Chifukwa chachikulu chopewera kukwiya n’chakuti timafuna kutsanzira Yehova yemwe “sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu.” (Sal. 103:10) Kupewa kukwiya kumatithandizanso m’njira zina. Munthu amene amakonda kukwiya akhoza kudwala matenda monga othamanga magazi kapena a m’mapapo. Akhozanso kudwala matenda a chiwindi, a mphafa kapena a m’mimba. Munthu akakwiya saganizanso bwino. Vuto lina ndi lakuti pambuyo pokwiya kwambiri, munthu akhoza kuvutika maganizo kwa nthawi yaitali. Koma Baibulo limanena kuti: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miy. 14:30) Ndiye kodi tingatani kuti tisakwiye ngati m’bale wathu watikhumudwitsa? Nanga tingatani kuti tikhazikitse mtendere ndi m’bale wathuyo? Kutsatira mfundo zanzeru za m’Baibulo n’kumene kungatithandize. w18.01 10 ¶14-15

Lachiwiri, January 8

Simudzasiya moyo wanga m’Manda. Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.​—Sal. 16:10.

Apa Davide sankatanthauza kuti iyeyo sadzamwalira kapena kuti sadzakhala m’manda. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Davide anakalamba n’kufa. Amasonyezanso kuti atafa “anagona limodzi ndi makolo ake, ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.” (1 Maf. 2:1, 10) Ndiye kodi lemba la Salimo 16:10 linalosera za ndani? Petulo anafotokoza lembali la Salimo 16:10 kwa Ayuda komanso anthu ena amene analowa Chiyuda. Anachita zimenezi patangopita milungu ingapo kuchokera pamene Yesu anaphedwa n’kuukitsidwa. (Mac. 2:29-32) Iye ananena kuti Davide anamwaliradi n’kuikidwa m’manda ndipo anthu amene ankamvetserawo ankadziwa bwino zimenezi. Baibulo silinena kuti anthuwo anatsutsa pamene Petulo ankanena kuti Davide “anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka” kwa Mesiya. Petulo anatsindika mfundo imeneyi ponena mawu a Davide pa Salimo 110:1. (Mac. 2:33-36) Iye anagwiritsa ntchito Malemba pothandiza anthuwo kuzindikira kuti Yesu anali “Ambuye ndi Khristu.” Ndipo anthuwo anavomerezanso kuti lemba la Salimo 16:10 linakwaniritsidwa pamene Yesu anaukitsidwa. w17.12 10 ¶10-12

Lachitatu, January 9

Zinthu zonsezo tinaziwerenga n’kuziyeza kenako tinalemba kulemera kwa zinthu zonsezo.​—Ezara 8:34.

Abale a m’Bungwe Lolamulira amapemphera ndiponso kuganizira kwambiri mmene angagwiritsire ntchito ndalama za gulu, n’cholinga choti achite zinthu mokhulupirika komanso mwanzeru. (Mat. 24:45) Iwo amapanga bajeti ndipo amaitsatira pogwiritsa ntchito ndalamazo. (Luka 14:28) Mtumwi Paulo anatenga ndalama zimene abale anapereka kuti zikathandize Akhristu a ku Yudeya. Iye anaonetsetsa kuti anthu amene anakapereka ndalamazo ‘azisamalire moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.’ (2 Akor. 8:18-21.) Masiku ano gulu lathu limatsanzira Ezara ndi Paulo poonetsetsa kuti zopereka zikugwiritsidwa ntchito moyenera. (Ezara 8:24-33) M’zaka zapitazi, gulu linayamba kuchita zinthu zina zatsopano. Limayesetsa kupeza njira zochepetsera ndalama zimene limagwiritsa ntchito pa zinthu zosiyanasiyana n’cholinga choti ndalama zimene mumapereka zizigwiritsidwa ntchito moyenera. w18.01 19-20 ¶12-13

Lachinayi, January 10

Mtendere wa Khristu ulamulire m’mitima yanu.—Akol. 3:15.

Chikondi komanso kukoma mtima, zingatithandize kuti tizikhululukirana. Mwachitsanzo, ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa, tizikumbukira nthawi zimene ifeyo tinachitanso zinthu zokhumudwitsa ena. Mosakayikira tinayamikira kwambiri chikondi ndi kukoma mtima zimene abale ndi alongowo anatisonyeza potikhululukira. (Mlal. 7:21, 22) Timayamikiranso kwambiri kukoma mtima kumene Khristu wasonyeza potithandiza kuti tizilambira Yehova mogwirizana. Tonsefe timakonda Mulungu mmodzi, timalalikira uthenga wofanana ndipo mavuto ambiri amene timakumana nawo ndi ofanananso. Tikamasonyeza chikondi ndiponso kukoma mtima pokhululukirana, timakhala ogwirizana ndipo timapewa zinthu zimene zingatilepheretse kudzalandira mphoto. M’Baibulo muli zitsanzo zosonyeza kuti nsanje ingatilepheretse kulandira mphoto. Mwachitsanzo, Kaini anachitira nsanje m’bale wake Abele ndipo anamupha. Kora, Datani ndi Abiramu anachitira nsanje Mose ndipo anayamba kutsutsana naye. Nayenso Sauli anachita nsanje kwambiri ataona zinthu zabwino zimene Davide anachita moti ankafuna kumupha. w17.11 27 ¶9-10

Lachisanu, January 11

Muzifunafuna, kufufuza ndi kufunsitsa za nkhani imeneyo.—Deut. 13:14.

Akulu akakhala pa komiti yoweruza ayenera kufufuza bwinobwino kuti aone ngati Mkhristu amene wachimwayo ali ndi mtima wolapa. Koma ayenera kukumbukira kuti si zapafupi kuzindikira ngati munthu walapadi. Pamafunika kudziwa maganizo komanso mtima umene munthuyo ali nawo. (Chiv. 3:3) Tikutero chifukwa munthu ayenera kulapa ndi mtima wonse kuti asonyezedwe chifundo. Mosiyana ndi Yehova ndi Yesu, akulu sangaone mumtima mwa munthu. Ngati ndinu mkulu, kodi mungadziwe bwanji ngati munthu walapa ndi mtima wonse? Choyamba, muyenera kupempha Mulungu kuti akuthandizeni kuchita zinthu mwanzeru ndiponso mozindikira. (1 Maf. 3:9) Chachiwiri, muyenera kufufuza m’Mawu a Mulungu komanso mabuku amene kapolo wokhulupirika watipatsa. Zimenezi zingakuthandizeni kuzindikira ngati munthuyo ali ndi “chisoni cha dziko” kapena walapadi ndipo ali ndi “chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” (2 Akor. 7:10, 11) Muyenera kuona mmene Baibulo limafotokozera anthu olapa ndiponso amene sanalape. Onani mmene limafotokozera mtima wawo, maganizo awo komanso khalidwe lawo. w17.11 17 ¶16-17

Loweruka, January 12

[Ana] adzakhala . . . osamvera makolo.​—2 Tim. 3:2.

N’zoona kuti anthu ambiri amaona kuti khalidwe limeneli si vuto ndipo mabuku, mafilimu ndiponso mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa ana kukhala osamvera. Koma khalidweli ndi limene limasokoneza mabanja ambiri. Anthu akhala akudziwa mfundo imeneyi kuyambira kalekale. Mwachitsanzo, kale ku Greece munthu akamenya makolo ake ankamulanda ufulu wake. Komanso ku Rome, munthu akamenya bambo ake ankalangidwa mofanana ndi amene wapha munthu. Malemba Achiheberi komanso Malemba Achigiriki amalangizanso ana kuti azilemekeza makolo awo. (Eks. 20:12; Aef. 6:1-3) Ana angapewe kutengera khalidwe la kusamvera akamaganizira zinthu zabwino zimene makolo awo awachitira. Angachitenso bwino kukumbukira kuti Mulungu, yemwe ndi Atate wa tonsefe, amatilamula kuti tikhale omvera. Ana akamalankhula zinthu zabwino zokhudza makolo awo, angathandize ana anzawo kuti azilemekezanso makolo awo. w18.01 29 ¶8-9

Lamlungu, January 13

Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.—Yes. 32:2.

Masiku ano, Mkhristu amene wachita tchimo lalikulu ayenera kufotokozera akulu kuti amuthandize. Kodi zimenezi ndi zofunika bwanji? Choyamba, Yehova ndi amene anakonza zoti akulu azitithandiza tikachimwa ndipo izi n’zogwirizana ndi zimene Mawu ake amanena. (Yak. 5:14-16) Chachiwiri, zimenezi zimapereka mwayi kwa wochimwayo kuti athandizidwe ndi Yehova komanso asakhale ndi chizolowezi chochimwa. (Agal. 6:1; Aheb. 12:11) Chachitatu, akulu anapatsidwa udindo komanso anaphunzitsidwa bwino kuti azitha kulimbikitsa munthu wochimwa amene walapa n’cholinga choti asamadziimbe mlandu kwambiri. Yehova ananena kuti akuluwo ali ngati “malo ousapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:2) Kodi inuyo simukuvomereza kuti Mulungu anasonyeza chifundo pokonza zoti ochimwa azithandizidwa ndi akulu? Atumiki a Yehova ambiri amene anachimwa n’kufotokozera akulu anathandizidwa ndipo mtima wawo unakhala m’malo. w17.11 10 ¶8-9

Lolemba, January 14

Chilango . . . chimakhala chowawa.​—Aheb. 12:11.

Ngakhale kuti zingakhale zopweteka, tiyenera kupewa kucheza ndi wachibale amene wachotsedwa, kaya polemberana makalata, mameseji, maimelo kapena njira zina. Koma tisataye mtima. Chikondi “chimayembekezera zinthu zonse,” kuphatikizapo kuyembekezera kuti anthu amene anasiya Yehova adzabwerera. (1 Akor. 13:7) Ngati mutaona kuti wachibale wanu wayamba kusintha mtima wake, mungamupempherere kuti apeze mphamvu kuchokera m’Malemba ndipo avomere pamene Yehova akumupempha kuti: “Bwerera kwa ine.” (Yes. 44:22) Yesu ananena kuti ngati timakonda munthu aliyense kuposa mmene timakondera iyeyo, ndiye kuti sitingakhale wotsatira wake. Komabe, sankakayikira kuti otsatira ake adzapitirizabe kukhala okhulupirika kwa iye ngakhale atamatsutsidwa ndi achibale awo. Ngati kutsatira Yesu kwabweretsa “lupanga” m’banja lanu, muyenera kudalira Yehova kuti akuthandizeni kupirira. (Yes. 41:10, 13) Muzisangalala podziwa kuti Yehova ndi Yesu akusangalala nanu ndipo adzakupatsani mphoto ngati mutakhalabe okhulupirika. w17.10 16 ¶19-21

Lachiwiri, January 15

Valani chifundo chachikulu.—Akol. 3:12.

Tikamaona anthu akuvutika chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu, timafuna kuwachitira chifundo. Tonsefe timalakalaka matenda ndi ukalamba zitatha. N’chifukwa chake timapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Komanso timachita zimene tingathe pothandiza anzathu amene akuvutika. Wolemba mabuku wina analemba zimene zinachitikira mayi ake amene anali okalamba komanso ankadwala matenda a mu ubongo. Tsiku lina anadziipitsira ndipo pamene ankayesetsa kuti akonze zovala zawo, anthu ena anagogoda pakhomo. Anthuwo anali a Mboni awiri omwe ankakonda kubwera kudzacheza nawo. Alongowo anafunsa mayiwo ngati pali chinachake chimene angawathandize. Mayiwo anayankha kuti, “Ee kungoti n’zochititsa manyazi.” Komabe alongowo anawathandiza bwinobwino. Kenako anapangira mayiwo tiyi ndipo anapitiriza kucheza nawo. Mwana wawoyo anayamikira kwambiri ndipo analemba kuti: “A Mboniwo anachita bwino kwambiri. Iwo amachitadi zinthu zimene amaphunzitsa.” Kodi inuyo mumachitira chifundo anthu odwala komanso okalamba n’kumachita zonse zimene mungathe powathandiza?​—Afil. 2:3, 4. w17.09 9 ¶5; 12 ¶14

Lachitatu, January 16

Tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18.

Ngati zingatheke, tingachite bwino kuthandiza abale athu m’njira zosaonekera kwa anthu. (Mat. 6:1-4) Tizikhalanso patsogolo posonyeza ulemu. (Aroma 12:10) Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza anthu ena posambitsa mapazi ophunzira ake. (Yoh. 13:3-5, 12-15) Tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa kuti tizitsanzira Yesu pa nkhani yolemekeza ena, ngakhale kuti nthawi zina zingativute. Paja nawonso ophunzira a Yesu sanamvetse chifukwa chake iye anawasambitsa mapazi, mpaka atalandira mzimu woyera. (Yoh. 13:7) Tingasonyeze kuti timalemekeza ena tikamapewa kudziona kuti ndife apamwamba chifukwa cha maphunziro athu, chuma chathu kapena udindo umene tili nawo m’gulu la Yehova. (Aroma 12:3) Nthawi zina anthu ena angayamikiridwe pa zinthu zimene ifeyo tikuona kuti tiyeneranso kuyamikiridwa. Zoterezi zikachitika tiyenera kusangalala nawo limodzi, osati kuwachitira nsanje. w17.10 9 ¶9-10

Lachinayi, January 17

Ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.​—1 Akor. 9:23.

Akhristu ambiri amaona kuti kuwerenga Baibulo mu utumiki kumathandiza kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina amene anachita ulendo wobwereza kwa munthu wina wachikulire. Munthuyo anali atawerenga magazini athu kwa zaka zambiri. M’malo mongomupatsa Nsanja ya Olonda yatsopano, m’baleyo anaganiza zomuwerengera lemba limene linali m’magaziniyo. Anamuwerengera lemba la 2 Akorinto 1:3, 4 lomwe limanena kuti: “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.” Wachikulireyo analikonda kwambiri lembali moti anapempha m’baleyo kuti aliwerengenso. Kenako ananena kuti iye ndi mkazi wake ankafunitsitsa kutonthozedwa. Zimenezi zinachititsa kuti afune kuphunzira zambiri. Uwutu ndi umboni wakuti Mawu a Mulungu amakhala amphamvu tikamawagwiritsa ntchito mu utumiki.​—Mac. 19:20. w17.09 26 ¶9-10

Lachisanu, January 18

Tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!​—Yobu 2:5.

N’zosachita kufunsa kuti angelo okhulupirika anakwiya kwambiri ndi zimene Satana anachita. N’kutheka kuti inunso zimakupwetekani mukaganizira mavuto ambirimbiri amene Satana anayambitsa. Yehova anafunika kuthetsa nkhani imeneyi koma sanachite zinthu mopupuluma. Iye anaiganizira bwinobwino n’kuchita zinthu moyenera. Sanakwiye msanga ndipo njira imene wasankha kuti athetsere nkhaniyi ndi yachilungamo. (Eks. 34:6; Yobu 2:2-6) Yehova walola kuti nthawi yaitali idutse chifukwa choti safuna kuti munthu aliyense awonongedwe koma kuti “anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Zimene Yehova anachita zikusonyeza kuti nafenso sitiyenera kuchita zinthu mopupuluma koma tiyenera kuganiza bwino tisanalankhule kapena kuchita chilichonse. Pakakhala nkhani yofunika kwambiri, tiyenera kudzipatsa nthawi yoti tiiganizire bwinobwino n’kuchita zinthu mwanzeru. Tiyeneranso kupempha Yehova kuti atipatse nzeru n’cholinga choti tilankhule komanso kuchita zinthu zoyenera. (Sal. 141:3) Munthu akachita zinthu asanaganize bwinobwino akhoza kulakwitsa kwambiri n’kudzadandaula pambuyo pake.​—Miy. 14:29; 15:28; 19:2. w17.09 4 ¶6-7

Loweruka, January 19

Chisoticho udzaveke Yoswa mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki.​—Zek. 6:11.

Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Yoswa anali mfumu? Ayi. Iye sanali mumzere wachifumu wa Davide choncho sanali woyenera kukhala mfumu. Koma zimene Zekariya anachitazo zinasonyeza kuti kudzabwera wina amene adzakhale mfumu mpaka kalekale komanso wansembe. Dzina la amene adzakhale mfumu komanso wansembeyo ndi Mphukira. Malemba amasonyeza kuti Yesu Khristu ndi amene ali Mphukira. (Yes. 11:1; Mat. 2:23) Yesu, yemwe ndi Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe, ndi amene akutsogolera gulu lankhondo la angelo. Iye amagwira ntchito mwakhama n’cholinga choti gulu la anthu a Mulungu likhale lotetezeka m’dziko loipali. (Yer. 23:5, 6) Posachedwapa, Khristu adzatsogolera pa ntchito yogonjetsa anthu oipa n’cholinga choti ateteze anthu a Mulungu komanso asonyeze kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. (Chiv. 17:12-14; 19:11, 14, 15) Koma Khristu, kapena kuti Mphukira, ali ndi zinthu zina zambiri zoti achite asanagonjetse adaniwo. w17.10 29 ¶12-14

Lamlungu, January 20

Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.​—Akol. 3:9.

Kodi mungatani ngati zovala zanu zada kwambiri mwina mpaka kufika ponunkha? Mukhoza kuvula zovalazo mwamsanga. Tingachitenso bwino kumvera mwamsanga lamulo loti tisiye makhalidwe akale omwe Mulungu sasangalala nawo. Tiyenera kumvera malangizo osapita m’mbali amene Paulo anauza Akhristu akale akuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu.” Tiyeni panopa tikambirane za zinthu ziwiri zimene Paulo ananena kuti tiyenera kusiya zomwe ndi dama ndiponso zinthu zodetsa. (Akol. 3:5-9) Mawu a m’Baibulo amene anawamasulira kuti “dama” amanena za kugonana pakati pa anthu amene sanakwatirane motsatira malamulo komanso pakati pa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha. Paulo anauza Akhristu anzake kuti ‘achititse ziwalo za thupi lawo kukhala zakufa ku dama’ kapena kuti asiyiretu kulakalaka chilichonse chokhudza dama. Mawu amene Paulo anagwiritsa ntchitowa akusonyeza kuti munthu ayenera kuchita zinthu mwamphamvu kuti asiye kulakalaka zoipa. Koma chomwe tiyenera kudziwa n’chakuti n’zotheka kuchita zimenezi. w17.08 18 ¶5-6

Lolemba, January 21

Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.​—Mika 7:7.

Zimene tikukumana nazo masiku ano zikufanana ndi zimene zinkachitika munthawi ya mneneri Mika. Iye anakhala pa nthawi imene Ahazi anali mfumu ndipo zinthu zambiri zopanda chilungamo zinkachitika. Baibulo limanena kuti anthu ‘ankachita zoipa ndipo ankazichita bwino kwambiri.’ (Mika 7:1-3) Mika anazindikira kuti palibe zimene iyeyo angachite kuti athetse mavutowa. Ngati tili ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Mika nafenso tidzakhala ndi mtima wofuna kuyembekezera Yehova. Sitili ngati mkaidi yemwe akudikira nthawi yoti aphedwe. Zinthu zimene akudikirazo sazifuna koma amangodikirabe chifukwa choti sangachitire mwina. Koma ifeyo timayembekezera Yehova chifukwa chodziwa kuti iye adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzatipatsa moyo wosatha pa nthawi yoyenera. Choncho ‘timapirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.’ (Akol. 1:11, 12) Koma tikamayembekezera kwinaku tikudandaula kuti Yehova akuchedwa kukwaniritsa malonjezo ake, iye sangasangalale nafe.​—Akol. 3:12. w17.08 4 ¶6-7

Lachiwiri, January 22

Yehova amathandiza anthu ofatsa.​—Sal. 147:6.

Kodi ifeyo tingatani kuti Mulungu azitithandiza? Chofunika ndi kukhala naye pa ubwenzi. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kuyesetsa kukhala anthu ofatsa. (Zef. 2:3) Munthu wofatsa amayembekezera Yehova kuti akonze zolakwika komanso athetse mavuto amene wakumana nawo. Ndiyeno Yehova amasangalala kwambiri ndi anthu oterewa. Koma Malemba amati Mulungu ‘amagwetsera pansi anthu oipa.’ (Sal. 147:6b) Mawuwatu ndi amphamvu kwambiri. Choncho kuti Yehova asatikwiyire koma azitikomera mtima, tiyenera kudana ndi zimene iye amadana nazo. (Sal. 97:10) Mwachitsanzo, tiyenera kudana ndi chiwerewere. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kudana ndi zinthu zilizonse zimene zingatipangitse kuchita chiwerewere. Zina mwa zinthu zimenezi ndi kuonera zolaula. (Sal. 119:37; Mat. 5:28) Kupewa zimenezi n’kovuta koma tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti Yehova atidalitse. Kuti tipambane pa nkhondo yolimbana ndi zinthu zimenezi tiyenera kudalira Yehova osati kudzidalira. Tiyenera kuchonderera Yehova kuti atithandize. w17.07 19-20 ¶11-13

Lachitatu, January 23

Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova.​—Miy. 19:17.

Munthu akamapereka chuma chake pothandiza ntchito za Ufumu amakhala akugwiritsa ntchito zinthu zake pothandiza ena. Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena ali ndi chuma koma sangakwanitse kuchita utumiki wa nthawi zonse kapena kusamukira kudziko lina. Koma ndalama zimene amapereka zimathandiza kuti anthu ena achite bwino utumiki wawo. Zopereka zathu zimathandiza kuti tizitha kusindikiza mabuku komanso kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino m’mayiko osauka komwe anthu ambiri akuphunzira Baibulo. Kwa zaka zambiri, m’mayiko ena monga ku Congo, ku Madagascar ndi ku Rwanda, Mabaibulo anali odula kwambiri moti abale ankafunika kugwira ntchito mlungu umodzi kapenanso mwezi wathunthu kuti apeze ndalama zogulira Baibulo. Ena ankalolera kuti asagule chakudya n’cholinga choti akhale ndi Baibulo. Koma panopa zinthu zasintha chifukwa cha zopereka za anthu ambiri komanso chifukwa choti gulu lathandiza kuti “pakhale kufanana” pa nkhani ya ndalama.​—2 Akor. 8:13-15. w17.07 9 ¶11

Lachinayi, January 24

Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.​—Miy. 27:11.

Kodi kuganizira ubwino wokhalabe okhulupirika kungatilimbikitse bwanji? Kungatithandize kuzindikira kuti mavuto athu amatipatsa mwayi wosonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova ndipo si umboni woti iye sakusangalala nafe. Paja Baibulo limanena kuti kupirira kumachititsa kuti “tikhale ovomerezeka kwa Mulungu” ndipo kumatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo champhamvu. (Aroma 5:3-5) Nkhani ya Yobu imasonyezanso kuti “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Choncho tisamakayikire kuti iye adzatidalitsa komanso adzadalitsa anthu onse amene ali kumbali ya ulamuliro wake. Kudziwa zimenezi kungatithandize “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.” (Akol. 1:11) N’zoona kuti kukumbukira nthawi zonse nkhani yofunika yokhudza ulamuliro wa Yehova si kophweka. Choncho ndi bwino kumadzikumbutsa nthawi ndi nthawi za kufunika kosonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova. w17.06 26 ¶15-16

Lachisanu, January 25

Chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.—Luka 12:15.

Masiku ano anthu ambiri amangokhalira kuganizira zinthu monga zovala ndiponso zipangizo zamakono zomwe zangotuluka kumene. N’chifukwa chake Mkhristu aliyense ayenera kudzifufuza pa nkhaniyi. Akhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti zinthu za m’dzikoli ndi zofunika kwambiri? Kodi nthawi yambiri ndimakhala ndikufufuza ndiponso kuganizira zinthu monga mafoni kapena zovala kuposa nthawi imene ndimakhala ndikukonzekera misonkhano? Kodi ndimatanganidwa kwambiri ndi zinthu za tsiku ndi tsiku moti sindikhala ndi nthawi yambiri yoti ndizipemphera kapena kuwerenga Baibulo?’ Tikaona kuti tikuyamba kukonda zinthu za m’dzikoli kuposa Khristu, tingachite bwino kuganizira mawu a Yesu amene ali mulemba lalero. Yesu ananena kuti “kapolo sangatumikire ambuye awiri.” Iye ananenanso kuti: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Zili choncho chifukwa “ambuye” onse sangafune kuti tizitumikiranso wina. (Mat. 6:24) Tonsefe ndife ochimwa choncho tiyenera kulimbana ndi “zilakolako za thupi lathu,” kuphatikizapo mtima wokonda chuma.​—Aef. 2:3. w17.05 25-26 ¶15-16

Loweruka, January 26

Ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.—1 Akor. 9:23.

Anthufe tili ngati zonyamulira zoumbidwa ndi dothi chifukwa si ife angwiro, koma uthenga umene timalalikira ukhoza kuthandiza ifeyo komanso anthu ena kuti adzapeze moyo wosatha. Mtumwi Paulo ankachita khama kwambiri pa ntchito yophunzitsa anthu chifukwa choti ankakonda utumiki. (Aroma 1:14, 15; 2 Tim. 4:2) Zimenezi zinamuthandizanso kuti apirire pa nthawi imene ankatsutsidwa kwambiri. (1 Ates. 2:2) Kodi ifenso tingasonyeze bwanji kuti timakonda utumiki? Paulo ankakhala tcheru nthawi zonse kuti aone mpata woti alalikire ndipo iyi ndi njira ina imene anasonyezera kuti ankakonda utumiki. Mofanana ndi atumwi komanso Akhristu ena oyambirira, timalalikira mwamwayi, m’malo opezeka anthu ambiri komanso kunyumba ndi nyumba. (Mac. 5:42; 20:20) Ngati n’zotheka, tingawonjezere utumiki wathu, mwina pochita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Tikhozanso kuphunzira chilankhulo china, kusamukira kudera lina kapenanso kudziko lina.​—Mac. 16:9, 10. w17.06 10-11 ¶8-9

Lamlungu, January 27

Phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zinachotsedwa m’malo awo.​—Chiv. 6:14.

Mavuto ambiri a m’dzikoli amayambitsidwa ndi mabungwe osati anthu paokha. Pali zipembedzo zambiri zimene zimanamiza anthu pa nkhani zokhudza Mulungu, Baibulo komanso tsogolo la anthu ndi dzikoli. Ndiye palinso maboma amene amalimbikitsa nkhondo, kusankhana mitundu, kupondereza osauka, ziphuphu komanso kukondera. Makampani ena amawononga zinthu zachilengedwe komanso kubera anthu pa nkhani za malonda. Izi zimachititsa kuti anthu ochepa azilemera kwambiri pomwe ochuluka ali pa umphawi. Choncho n’zosachita kufunsa kuti mabungwe ambiri akuyambitsa mavuto m’dzikoli. Baibulo linaneneratu kuti maboma onse ndiponso mabungwe amene amagwirizana nawo potsutsa Ufumu wa Mulungu adzawonongedwa. Chimenechi chidzakhala chimake cha chisautso chachikulu.​—Yer. 25:31-33. w17.04 11 ¶7-8

Lolemba, January 28

Sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake.​—1 Maf. 21:29.

Yehova “amayesa mitima” ndipo anasonyeza chifundo kwa Ahabu. (Miy. 17:3) Achibale komanso anzake a Naboti atamva kuti Mulungu sapereka chilango ku banja la Ahabu mpaka Ahabuyo adzamwalire, ziyenera kuti zinawavuta kumvetsa. Koma kudzichepetsa ndi komwe kukanawathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova podziwa kuti iye sangachite zinthu zopanda chilungamo. (Deut. 32:3, 4) Yehova adzaukitsa Naboti ndi ana ake ndipo iwo ndi achibale awo adzasangalala kuona kuti Yehova ndi wachilungamo. (Yobu 14:14, 15; Yoh. 5:28, 29) Komanso munthu wodzichepetsa amakumbukira kuti “Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.” (Mlal. 12:14) Izi zikusonyeza kuti Yehova akamapereka chiweruzo amaganizira mfundo zonse ndipo zina zimakhala zoti ifeyo sitikuzidziwa. Choncho kudzichepetsa kungatithandize kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova. w17.04 24 ¶8-9

Lachiwiri, January 29

Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.​—Miy. 17:17.

Chifukwa cha mmene zinthu zilili m’dzikoli, abale athu ambiri amathawira m’mayiko ena. Zimenezi zingakhale zovuta kwambiri. Tangoganizirani zinthu zimene anthuwa mwina ayenera kusintha pa nthawi imodzi. Ayenera kuphunzira chinenero ndi chikhalidwe chatsopano. Ayeneranso kutsatira malamulo atsopano pa nkhani monga misonkho, njira zolipirira zinthu, kupita kusukulu komanso kulera ana. Choncho mungachite bwino kwambiri kukhala oleza mtima ndiponso aulemu pothandiza abale ndi alongo amene akukumana ndi zimenezi. (Afil. 2:3, 4) Nthawi zina zimene maboma amachita zimachititsa kuti abalewa azivutika kupeza a Mboni m’dziko limene athawira. Komanso abale akakana kugwira ntchito ina chifukwa chosafuna kujomba kumisonkhano, mabungwe ena amanena kuti saziwathandiza. Izi zachititsa kuti abale ena agonje chifukwa cha mantha. Choncho tiyenera kuyesetsa kukumana mwamsanga ndi abale ndi alongo amene athawira m’dziko lathu. Abalewa amafunikira kudziwa kuti timawakonda kwambiri. Tikamawathandiza ndiponso kuwachitira chifundo, akhoza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.​—Miy. 12:25. w17.05 5 ¶9-10

Lachitatu, January 30

Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.—Mat. 24:12.

Pofotokoza chizindikiro cha “mapeto a nthawi ino,” Yesu ananena kuti “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mat. 24:3) M’nthawi ya atumwi, Ayuda omwe ankati ndi anthu a Mulungu analola kuti chikondi chawo chizirale ndipo anasiya kukonda kwambiri Mulungu. Koma Akhristu ambiri ankakonda kwambiri Mulungu, Akhristu anzawo komanso anthu ena ndipo ankalalikira mwakhama “uthenga wabwino wonena za Khristu.” (Mac. 2:44-47; 5:42) Ngakhale zinali choncho, panalinso Akhristu ena amene analola kuti chikondi chawo chizirale. Yesu Khristu ataukitsidwa anauza mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.” (Chiv. 2:4) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti asinthe? Mwina anasokonezedwa ndi anthu okonda zinthu za m’dziko.​—Aef. 2:2, 3. w17.05 17-18 ¶1-3

Lachinayi, January 31

Uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.​—Mat. 5:33.

Yefita anali mtsogoleri wamphamvu komanso msilikali wolimba mtima. Hana ankagonjera mwamuna wake ndiponso ankasamalira bwino banja lake. Anthu awiri onsewa ankalambira Yehova ndipo anachita zinthu zina zofanana. Onse analonjeza Yehova zinazake ndipo anazikwaniritsa. Masiku ano, anthu amene amalonjeza zinazake kwa Yehova akhoza kuphunzira zambiri kwa anthu awiriwa. Baibulo limasonyeza kuti pali zinthu zosiyanasiyana zimene munthu angalonjeze kwa Mulungu. Angalonjeze kuti achita zinazake, apereka mphatso inayake, achita utumiki winawake kapena azipewa zinthu zinazake. Munthu amalonjeza zinthu ngati zimenezi mwa kufuna kwake osati mokakamizidwa. Koma malonjezo oterewa amakhala opatulika chifukwa chakuti munthuyo amakhala kuti walumbira pamaso pa Mulungu kuti azichita kapena sazichita zinazake.​—Gen. 14:22, 23; Aheb. 6:16, 17. w17.04 3 ¶1-2

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena