Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kabukuka
M’masamba otsatirawa muona kuti tsiku lililonse lili ndi lemba lake komanso ndemanga yake. Ngakhale kuti mukhoza kupanga lemba la tsiku nthawi ina iliyonse, ena amaona kuti zimakhala zothandiza kwambiri kupanga m’mawa. Zimenezi zimawathandiza kuti aziganizira mfundo za m’lembalo tsiku lonse. Kupanga lemba la tsiku ndi banja lanu n’kothandizanso kwambiri. Anthu otumikira pa Beteli padziko lonse amakambirana lemba la tsiku pa nthawi ya chakudya cham’mawa.
Ndemangazi zachokera mu Nsanja ya Olonda (w) ya April 2017 mpaka ya March 2018. Manambala olembedwa kumapeto kwa deti la magazine a Nsanja ya Olonda ndi a tsamba limene pachokera ndemanga ndipo nambala yotsatira ndi ya ndime zimene pachokera ndemangayo. (Onani chitsanzo m’munsimu.) Mfundo zina zogwirizana ndi lembali mungazipeze munkhaniyo.