Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 118-128
  • December

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Lamlungu, December 1
  • Lolemba, December 2
  • Lachiwiri, December 3
  • Lachitatu, December 4
  • Lachinayi, December 5
  • Lachisanu, December 6
  • Loweruka, December 7
  • Lamlungu, December 8
  • Lolemba, December 9
  • Lachiwiri, December 10
  • Lachitatu, December 11
  • Lachinayi, December 12
  • Lachisanu, December 13
  • Loweruka, December 14
  • Lamlungu, December 15
  • Lolemba, December 16
  • Lachiwiri, December 17
  • Lachitatu, December 18
  • Lachinayi, December 19
  • Lachisanu, December 20
  • Loweruka, December 21
  • Lamlungu, December 22
  • Lolemba, December 23
  • Lachiwiri, December 24
  • Lachitatu, December 25
  • Lachinayi, December 26
  • Lachisanu, December 27
  • Loweruka, December 28
  • Lamlungu, December 29
  • Lolemba, December 30
  • Lachiwiri, December 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 118-128

December

Lamlungu, December 1

Muzicherezana popanda kudandaula.​—1 Pet. 4:9.

Kale anthu ankasonyeza mtima wochereza poitanira anthu kunyumba kwawo kuti adzadye chakudya. (Gen. 18:1-8; Ower. 13:15; Luka 24:28-30) Munthu akachita zimenezi ankasonyeza kuti akufuna kuti amene wamuitanayo akhale mnzake komanso akhale naye pamtendere. Koma kodi tiyenera kuyamba ndi kuitana anthu ati? Tiyenera kuyamba ndi abale ndi alongo amumpingo wathu. Tikutero chifukwa tikadzakumana ndi mavuto aakulu tidzafunika kudalirana. Choncho tingachite bwino kuti tizikhala nawo mwamtendere komanso kugwirizana kwambiri. Oyang’anira madera, abale ndi alongo amene amapita kusukulu zophunzitsa Baibulo kapena kukathandiza ntchito zomangamanga angafunike malo ogona. Komanso pakachitika ngozi zadzidzidzi, mabanja ena amafunika malo ogona mpaka pamene nyumba zawo zakonzedwa. Sikuti anthu opeza bwino okhaokha ndi amene ayenera kuchereza alendo. Tikutero chifukwa chakuti mwina iwo achita zimenezi maulendo ambirimbiri. Choncho ngakhale titapanda kukhala ndi nyumba yabwino, tikhozabe kuitana anthu kuti afikire kwathu. w18.03 15 ¶6, 9

Lolemba, December 2

Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.​—Miy. 24:16.

Munthu akagwa sangathe kudzukanso payekha koma mzimu wa Mulungu ndi umene ungamuthandize. (Afil. 4:13) Ndipo khalidwe lina limene mzimuwo umatithandiza kukhala nalo ndi kudziletsa. Zinthu zina zimene zingatithandize kuti tizitha kudziletsa ndi kupemphera kuchokera pansi pa mtima, kuphunzira Baibulo ndiponso kuganizira kwambiri zimene tikuphunzira. Koma kodi tingatani ngati kuphunzira Mawu a Mulungu kumativuta? N’kutheka kuti mumaona kuti mulibe mtima wokonda kuphunzira. Koma dziwani kuti Yehova akhoza kukuthandizani ngati mungamulole kuti akuthandizeni. Iye angakuchititseni kuti “muzilakalaka” Mawu ake. (1 Pet. 2:2) Choyamba, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala odziletsa kuti muzipeza mpata wophunzira Mawu ake. Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi zimene mumapempha. Mwachitsanzo, muziphunzira Mawuwo mwina kwa nthawi yochepa chabe. Pakamapita nthawi, mwina kuphunzirako kungayambe kukusangalatsani ndipo simungaone kuti n’kovuta. Mukhoza kufika pomakonda kwambiri kukhala panokha n’kumaphunzira komanso kusinkhasinkha mfundo zamtengo wapatali zochokera kwa Yehova.​—1 Tim. 4:15. w18.03 29 ¶5-6

Lachiwiri, December 3

Chikupulumutsanso inuyo tsopano . . . ndicho ubatizo.—1 Pet. 3:21.

Munthu asanabatizidwe ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Chikhulupirirochi angakhale nacho akadziwa bwino Mulungu, cholinga chake komanso zimene wakonza kuti apulumutse anthu. (1 Tim. 2:3-6) Chikhulupiriro choterechi chimathandiza munthu kuti azitsatira mfundo zachilungamo za Mulungu n’kumapewa makhalidwe amene Mulungu amadana nawo. (Mac. 3:19) Choncho sizingakhale zomveka kuti munthu adzipereke kwa Mulungu kwinaku akuchita zinthu zimene zingamulepheretse kudzalowa mu Ufumu. (1 Akor. 6:9, 10) Koma pali zinthu zinanso zofunika kuwonjezera pa kutsatira mfundo za Mulungu. Munthu amene akufuna kusangalatsa Yehova amayesetsa kupezeka pamisonkhano ya mpingo komanso kugwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mac. 1:8) Pambuyo pochita zimenezi, munthu akhoza kukhala woyenera kudzipereka kwa Mulungu m’pemphero kenako n’kubatizidwa posonyeza kuti anadzipereka. w18.03 6 ¶12

Lachitatu, December 4

[Mariya] anasunga . . . mawu onsewa mumtima mwawo.—Luka 2:51.

N’chifukwa chiyani Yehova anasankha Mariya kuti akhale mayi a Yesu? N’zosakayikitsa kuti anamusankha chifukwa anali munthu wauzimu. Zinthu zabwino zimene iye ananena poyamikira Mulungu, pamene anali kunyumba ya Zekariya ndi Elizabeti, zimasonyeza kuti anali wauzimu. (Luka 1:46-55) Zimene ananenazo zimasonyeza kuti ankakonda kwambiri Mawu a Mulungu komanso ankadziwa bwino Malemba Achiheberi. (Gen. 30:13; 1 Sam. 2:1-10; Mal. 3:12) Kumbukiraninso kuti iye ndi Yosefe atakwatirana sanagonane mpaka pamene Yesu anabadwa. Izi zikusonyeza kuti onse ankaganizira kwambiri za cholinga cha Mulungu osati kuchita zimene ankalakalaka. (Mat. 1:25) Mariya ankaonetsetsa zimene zinkachitika pa moyo wa Yesu ndipo ankamvetsera mawu anzeru amene ankalankhula. Iye ankachita chidwi kwambiri kuti aone mmene Mulungu akukwaniritsira malonjezo ake okhudza Mesiya. Kunena zoona, chitsanzo cha Mariya chimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tiziika cholinga cha Mulungu pamalo oyamba. w18.02 21 ¶11

Lachinayi, December 5

[Yobu] ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima.—Yobu 1:8.

Kodi tingachite chiyani kuti tikhale okhulupirika ndi omvera ngati Yobu? Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tiyenera kuika patsogolo zofuna za Yehova ndipo tizimukhulupirira komanso kumumvera ndi mtima wonse. Ndipotu ifeyo tili ndi zifukwa zambiri zochitira zimenezi kuposa Yobu. Mwachitsanzo, timadziwa zambiri zokhudza Satana komanso ziwembu zake. (2 Akor. 2:11) Ndipo Baibulo, makamaka buku la Yobu, limatithandizanso kumvetsa chifukwa chake Yehova amalola kuti tizivutika. Ulosi wa Danieli umatithandizanso kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma limene wolamulira wake ndi Khristu Yesu. (Dan. 7:13, 14) Komanso tikudziwa kuti Ufumu umenewu udzathetsa mavuto athu onse posachedwapa. Nkhani ya Yobu imatiphunzitsanso kuti tiyenera kuchitira chifundo Akhristu anzathu amene akuvutika. Mofanana ndi Yobu, ena angalankhule zinthu mosaganiza. (Mlal. 7:7) Koma m’malo mowaimba mlandu, tiyenera kuwamvetsa komanso kuwachitira chifundo. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikutsanzira Yehova yemwe ndi Atate wathu wachifundo.​—Sal. 103:8. w18.02 6 ¶16; 7 ¶19-20

Lachisanu, December 6

Kudzichepetsa kwanu n’kumene kudzandikweza.​—Sal. 18:35.

Anthu ena amayamba kunyada chifukwa cha zinthu monga kuoneka bwino, kutchuka, luso loimba kapena udindo wapamwamba. Davide anali ndi zinthu zonsezi koma anakhala wodzichepetsa kwa moyo wake wonse. Iye atapha Goliyati, Mfumu Sauli anamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire. Koma Davide ananena kuti: “Ndine yani ine, . . . kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?” (1 Sam. 18:18) Masiku ano, anthu a Yehova amayesetsa kukhala odzichepetsa ngati mmene ankachitira Davide. Timatsanzira Yehova, yemwe ndi Munthu wamkulu m’chilengedwe chonse, koma amadzichepetsa. Timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:12) Timadziwanso kuti chikondi ‘sichidzitama ndiponso sichidzikuza.’ (1 Akor. 13:4) Ndipo tikamayesetsa kukhala odzichepetsa, anthu ena angafune kuyamba kuphunzira za Yehova w18.01 28 ¶6-7

Loweruka, December 7

Anapitiriza kutipempha mochokera pansi pa mtima mochonderera kwambiri, kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo.​—2 Akor. 8:4.

Masiku anonso, tingapemphedwe kuti tipereke ndalama pothandiza pa ntchito zapadera. (Mac. 4:34, 35; 1 Akor. 16:2) Mwachitsanzo, mwina mpingo wanu ukukonzekera kuti umange Nyumba ya Ufumu. Kapena mwina Nyumba ya Ufumu yanu ikukonzedwa. Apo ayi, tikhoza kuuzidwa kuti pakufunika ndalama zoti msonkhano waukulu uchitike kapena kuti abale athu amene akumana ndi ngozi athandizidwe. Timaperekanso ndalama zothandiza kuti abale ndi alongo amene amagwira ntchito kulikulu lathu kapena kumaofesi a nthambi azisamaliridwa. Zopereka zathu zimathandizanso posamalira amishonale, apainiya apadera ndiponso oyang’anira madera ndi akazi awo. Aliyense wa ife angapereke ndalama pothandiza pa ntchito ya Yehova m’masiku otsiriza ano. Ambirife timapereka ndalama popanda ena kudziwa. Timaponya ndalamazo m’mabokosi a ku Nyumba ya Ufumu kapena timapereka kudzera pawebusaiti yathu ya jw.org. Tikhoza kuganiza kuti ndalama zochepa zimene timapereka n’zosathandiza kwenikweni. Komatu ndalama za gulu lathu zimachokera kwa anthu ambiri amene amapereka zochepa, osati kwa anthu ochepa amene amapereka zambiri. w18.01 19 ¶10-11

Lamlungu, December 8

Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano. Chimenechi ndicho ubatizo.—1 Pet. 3:21.

Mkhristu aliyense amafunika kubatizidwa kuti adzapulumuke. (Mat. 28:19, 20) Pamene munabatizidwa munasonyeza kuti mwadzipereka kwa Yehova. Munalonjeza Yehova kuti muzimukonda komanso muziika zofuna zake patsogolo nthawi zonse. Lonjezo limenelitu ndi lalikulu kwambiri. Koma simuyenera kuganiza kuti munalakwitsa kulipanga. Simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono chifukwa chodzipereka m’manja mwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene sakutumikira Yehova amalamuliridwa ndi Satana. Ndipo Satanayo safunira anthu zabwino. Iye angasangalale mutakana ulamuliro wa Yehova n’kukhala kumbali yake ndipo pa mapeto pake musadzapeze moyo wosatha. Koma taganizirani madalitso amene muli nawo chifukwa chodzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Popeza munapereka moyo wanu kwa Yehova, mukhoza kunena molimba mtima kwambiri kuti: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?” (Sal. 118:6) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala kumbali ya Yehova n’kumadziwa kuti akusangalala nanu. w17.12 23-24 ¶1-3

Lolemba, December 9

Usapse mtima kuti ungachite choipa.​—Sal. 37:8.

Nthawi zina Akhristu anzathu akhoza kutikhumudwitsa kapena ifeyo tikhoza kuwakhumudwitsa. Nkhani ngati zimenezi zikachitika zingakhale zovuta kupirira. Koma mofanana ndi mayesero ena, Yehova amalola kuti zimenezi zichitike. Iye amafuna kuti tisonyeze kuti ndife okhulupirika. Amafunanso kuti tiphunzire kugwira ntchito mogwirizana ndi anthu amene iye amawakonda ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina. Nkhani ya Yosefe imasonyeza kuti Yehova amatha kulola kuti atumiki ake akumane ndi mayesero. Yosefe ali wachinyamata, abale ake ankamuchitira nsanje moti anamugulitsa ndipo anakakhala kapolo ku Iguputo. (Gen. 37:28) Yosefe anali munthu wolungama komanso mnzake wa Mulungu. Choncho Yehova ayenera kuti anadandaula kwambiri kuona zoipa zimene zinkamuchitikira. Komabe, sanaletse kuti zimenezi zichitike. Pa nthawi ina Yosefe anaimbidwa mlandu woti ankafuna kugwiririra mkazi wa Potifara ndipo anamangidwa. Koma Yehova sanaletsenso zimenezi. Kodi izi zikutanthauza kuti Mulungu anamuiwala? Ayi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene [Yosefe] anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.”​—Gen. 39:21-23. w18.01 9-10 ¶12-14

Lachiwiri, December 10

Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke.—1 Akor. 15:13.

Kodi munganene kuti mfundo zikuluzikulu zimene mumakhulupirira ndi ziti? N’zosakayikitsa kuti munganene kuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse komanso kutipatsa moyo. Munganenenso kuti Yesu Khristu anafa kuti apereke dipo lotiwombola. Simungalepherenso kunena kuti m’tsogolomu dzikoli lidzakhala paradaiso ndipo anthu a Mulungu adzakhalamo kwamuyaya. Koma kodi mfundo yoti akufa adzauka mungaiikenso m’gululi? Ngakhale kuti tikuyembekezera kupulumuka chisautso chachikulu n’kulowa m’dziko latsopano, tili ndi zifukwa zomveka zonenera kuti kuuka kwa akufa ndi mfundo yofunika kwambiri pa chikhulupiriro chathu. Kunena zoona zikanakhala kuti Khristu sanauke ndiye kuti sakanakhala Mfumu yathu ndipo zonse zimene timaphunzitsa pa nkhani ya ulamuliro wa Khristu zikanakhala zopanda ntchito. (1 Akor. 15:12-19) Koma timadziwa kuti Yesu anaukitsidwa ndipo sitisiya kukhulupirira ndi mtima wonse zoti akufa adzauka.​—Maliko 12:18; Mac. 4:2, 3; 17:32; 23:6-8. w17.12 8 ¶1-2

Lachitatu, December 11

Mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo [ndi] chifundo.​—Mat. 23:23.

Afarisi ankangoona kukula kwa tchimo limene munthu wachita, osati mtima umene munthu wolakwayo anali nawo. Pa nthawi ina ataona kuti Yesu akudya kunyumba kwa Mateyu anafunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?” Yesu atamva zimenezo anayankha kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Mat. 9:9-13) Kodi pamenepa tinganene kuti Yesu ankalekerera anthu ochimwa? Ayi sitingatero. Tisaiwale kuti Yesu akamalalikira ankauzanso anthu ochimwa kuti alape. (Mat. 4:17) Koma iye anazindikira kuti anthu ena amene anali ‘okhometsa misonkho komanso ochimwa’ anali ndi mtima wofuna kusintha. Sikuti kunyumba ya Mateyu anthuwo anangopitira kukadya, chifukwa Baibulo limasonyeza kuti ena mwa anthuwo ankafuna kutsatira Yesu. (Maliko 2:15) N’zomvetsa chisoni kuti Afarisi ambiri sankaona anthu ngati amenewo mmene Yesu ankawaonera. w17.11 13 ¶2; 16 ¶15

Lachinayi, December 12

Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.​—Akol. 3:14.

Tonsefe timadziwa kuti ndi mwayi waukulu kukhala mumpingo wachikhristu. Tikamaphunzira limodzi Mawu a Mulungu kumisonkhano komanso kulimbikitsana timathandizidwa kuika maganizo athu pa mphoto imene tikuyembekezera. Koma nthawi zina tingakumane ndi mavuto chifukwa chosemphana maganizo ndi Akhristu anzathu. Tikapanda kuthetsa mwamsanga mavuto oterewa tikhoza kuyamba kusungirana chakukhosi. (1 Pet. 3:8, 9) Kodi tingatani kuti kusemphana maganizo ndi Akhristu anzathu kusadzatilepheretse kulandira mphoto? Paulo anauza Akhristu a ku Kolose kuti: “Monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu, oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”​—Akol. 3:12-13. w17.11 27 ¶7-8

Lachisanu, December 13

Azithawira kumzinda umodzi mwa mizindayi.—Yos. 20:4.

Munthu amene wapha mnzake mwangozi akafika pageti lolowera mumzinda wothawirako, ankafunika ‘kufotokoza nkhani yake kwa akulu.’ Ndipo akuluwo ankafunika kumulandira bwino. Koma pakapita nthawi, ankamubweza kumzinda umene anaphera munthuyo kuti akulu amumzindawo aweruze mlandu wake. (Num. 35:24, 25) Oweruzawo akapeza kuti munthuyo anaphadi mnzake mwangozi ankamulola kuti abwerere kumzinda wothawirako kuja. Kodi n’chifukwa chiyani ankafunika kufotokoza nkhani yake kwa akulu? Izi zinkathandiza kuti dziko la Isiraeli likhale losaipitsidwa komanso kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo achitiridwe chifundo ndi Yehova. Katswiri wina wa Baibulo analemba kuti ngati munthu wopalamula mlanduyo sanapite kwa akulu “zinkamuvuta yekha . . . chifukwa sanachite zonse zofunika kuti Mulungu amuteteze.” Akapanda kuthawira kumzinda wothawirako ndiye kuti ankatha kuphedwa ndi wachibale wapafupi wa munthu amene anaphedwayo. w17.11 9 ¶6-7

Loweruka, December 14

Kodi angelo onse si mizimu yotumikira ena, yotumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo?—Aheb. 1:14.

Yehova amagwiritsabe ntchito angelo ake kuti ateteze anthu ake komanso awalimbikitse. (Mal. 3:6; Aheb. 1:7) Kuchokera nthawi imene Isiraeli wauzimu anamasulidwa mu Babulo Wamkulu mu 1919, kulambira koona kwakhala kukuyenda bwino ngakhale kuti pali anthu ambiri otsutsa. (Chiv. 18:4) Mfundo yoti angelo amatiteteza imasonyeza kuti n’zosatheka kuti tidzakhalenso mu ukapolo wauzimu. (Sal. 34:7) Tisamakayikirenso kuti zinthu zidzapitiriza kutiyendera bwino mwauzimu padziko lonse. Paja pali gulu la nkhondo limene likutiteteza. Pa nthawi ya chisautso chachikuluyi, gulu la angelo a Yehova lidzafika kuti lititeteze ndipo lidzapha anthu onse otsutsana ndi ulamuliro wa Yehova. (2 Ates. 1:7, 8) Tsiku limenelo lidzakhala losaiwalika. w17.10 28 ¶10-11

Lamlungu, December 15

[Mudzilimbitse] pamaziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana, ndi kupemphera mu mphamvu ya mzimu woyera.​—Yuda 20.

Wachibale wathu akachotsedwa kapena akadzilekanitsa ndi mpingo, zimakhala zopweteka kwambiri ngati kuti wina watilasa ndi lupanga. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira ngati zimenezi zachitika? Simuyenera kusiya kuchita zinthu zokhudza kulambira. Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu powerenga Baibulo nthawi zonse, kukonzekera ndiponso kupezeka pamisonkhano yachikhristu, kugwira nawo ntchito yolalikira ndiponso kupemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kupirira. (Yuda 21) Koma bwanji ngati mukudzimva kuti mukungochita zinthuzo mwamwambo chabe? Musataye mtima. Kupitirizabe kuchita zinthu zauzimu kungathandize kuti maganizo anu akhalenso m’malo. Taganizirani chitsanzo cha munthu amene analemba Salimo 73. Iye anayamba kuona zinthu molakwika ndipo zinamuvutitsa kwambiri. Koma anasintha mmene ankaonera zinthu atafika pamalo olambirira Mulungu. (Sal. 73:16, 17) Nanunso zingakuyendereni bwino ngati mutapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. w17.10 16 ¶17-18

Lolemba, December 16

Chikondi chanu chisakhale cha chiphamaso.​—Aroma 12:9.

M’munda wa Edeni, Satana ananamizira kuti akuthandiza Hava koma anali wodzikonda ndipo zimene ankachitazo zinali zachinyengo. (Gen. 3:4, 5) Nayenso Ahitofeli sanasonyeze chikondi chenicheni kwa Davide ndipo anamuchitira chiwembu poganiza kuti akatero zimuyendera bwino. (2 Sam. 15:31) Masiku anonso, anthu ampatuko komanso anthu ena amene amasokoneza mtendere mumpingo amalankhula “mawu okopa ndi achinyengo” n’cholinga choti anthu aziganiza kuti amawakonda koma amachita zimenezi ali ndi zolinga zoipa. (Aroma 16:17, 18) Kusonyeza chikondi chachinyengo n’koipa kwambiri chifukwa munthu wochita zimenezi amanamizira kuti akusonyeza chikondi chochokera kwa Mulungu. Chinyengo chimenechi chikhoza kupusitsa anthu koma osati Yehova. Ndipotu Yesu ananena kuti anthu achinyengo adzalandira “chilango choopsa.” (Mat. 24:51) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimasonyeza chikondi chenicheni nthawi zonse kapena nthawi zina ndimakhala ndi kamtima kodzikonda kapena kachinyengo?’ w17.10 8 ¶6-8

Lachiwiri, December 17

Ndi odzipereka potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.—Aroma 10:2.

Tikamawerenga Mawu a Mulungu mu utumiki timakhala ngati tikupatsa Yehova mpata woti alankhule ndi munthuyo. Lemba losankhidwa bwino likhoza kuthandiza kwambiri munthu kuposa mawu alionse amene ifeyo tingalankhule. (1 Ates. 2:13) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kuwerengera Baibulo anthu amene ndimawalalikira?’ Komabe, kungowerengera munthu lemba si kokwanira. Tikutero chifukwa chakuti anthu ambiri salimvetsa bwino Baibulo. Vuto limeneli linalipo nthawi ya atumwi ndipo liliponso masiku ano. Choncho tisamaganize kuti tikangowerengera munthu lemba ndiye kuti adzamvetsa tanthauzo lake. Tiyenera kusankha mawu ofunika kwambiri palembalo, mwina n’kuwawerenganso kenako n’kufotokoza tanthauzo lake. Tikatero tidzathandiza kuti uthenga wa m’Baibulo ufike m’maganizo komanso mumtima mwa anthu amene tikukambirana nawo.​—Luka 24:32. w17.09 25 ¶7-8

Lachitatu, December 18

Mukhale . . . achifundo chachikulu.​—1 Pet. 3:8.

Anthu amene amayesetsa kutsanzira Yesu ayenera kusonyeza chifundo kwa Akhristu anzawo komanso kwa anthu ena. (Yoh. 13:34, 35) Mawu oti chifundo amatanthauzanso “kuvutikira limodzi ndi ena.” Choncho munthu wachifundo amamvera ena chisoni akamavutika ndipo amawathandiza. Inunso muziyesetsa kupeza njira zimene mungachitire zimenezi. Anthu ambiri amachitira chifundo anzawo akakumana ndi ngozi. Ndipo anthu a Yehova amadziwika kuti zoterezi zikachitika, amathandiza kwambiri. (1 Pet. 2:17) Mwachitsanzo, mlongo wina ku Japan ankakhala kudera limene kunasefukira madzi chifukwa cha chivomerezi mu 2011. Iye ananena kuti ‘analimbikitsidwa kwambiri’ ataona anthu ambiri ochokera ku Japan komweko komanso kumayiko ena atabwera kudzathandiza kukonza zinthu zimene zinawonongeka. Iye analemba kuti: “Zimenezi zinandithandiza kudziwa kuti Yehova amatikonda. Ndinaonanso kuti abale ndi alongo apadziko lonse amatikonda komanso amatipempherera.” w17.09 11 ¶12-13

Lachinayi, December 19

Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo . . . kudziletsa.​—Agal. 5:22, 23.

Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala odziletsa? Tiyeni tikambirane zifukwa ziwiri. Choyamba, anthu odziletsa sakumana ndi mavuto ambiri poyerekezera ndi amene sadziletsa. Komanso amakhala ndi anzawo odalirika, sakhala okwiya, sada nkhawa kwambiri komanso sakhumudwa mofanana ndi anthu osadziletsa. Chachiwiri, Mulungu amasangalala ndi anthu amene amatha kudziletsa komanso amene sagonja akamayesedwa. Nkhani ya Adamu ndi Hava imasonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona. (Gen. 3:6) Tangoganiziraninso za mavuto amene anthu ambirimbiri akhala akukumana nawo kuchokera nthawi ya Adamu ndi Hava chifukwa cholephera kudziletsa. Popeza anthufe si angwiro nthawi zina timalephera kudziletsa. Yehova amadziwa zimenezi ndipo amafunitsitsa kutithandiza kuti tisamachite zinthu zoipa zimene timalakalaka.​—1 Maf. 8:46-50. w17.09 4 ¶3-4

Lachisanu, December 20

Muvale umunthu watsopano.—Akol. 3:10.

Ku South Africa m’mbuyomo, a Mboni osiyana khungu sankaloledwa kuti azisonkhana limodzi. Koma Lamlungu pa 18 December 2011, zinali zosangalatsa kuona abale ndi alongo oposa 78,000 a mitundu yosiyanasiyana a ku South Africa komweko komanso akumayiko ena atasonkhana musitediyamu yaikulu kwambiri ku Johannesburg kuti aphunzitsidwe ndi Yehova. Mmodzi wa akuluakulu a pasitediyamuyo anati: “Sindinaonepo gulu la anthu amakhalidwe abwino ngati limeneli musitediyamuyi. Onse avala bwino kwambiri ndipo ayeretsa bwino malowa. Koma chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti alipo a mitundu yosiyanasiyana.” Mawu ngati amenewa amasonyezeratu kuti mgwirizano wathu padziko lonse ndi wapadera kwambiri. (1 Pet. 5:9) Koma kodi n’chiyani chimatithandiza kukhala osiyana ndi magulu ena? Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera zimatithandiza kuti tiziyesetsa ‘kuvula umunthu wakale n’kuvala umunthu watsopano.’​—Akol. 3:9. w17.08 17-18 ¶2-3

Loweruka, December 21

Nanunso khalani oleza mtima.—Yak. 5:8.

Baibulo limasonyeza kuti kuleza mtima ndi khalidwe limene mzimu woyera umatulutsa. Choncho popanda kuthandizidwa ndi Mulungu, munthu yemwe si wangwiro sangakhale woleza mtima bwinobwino. Mulungu ndi amene amathandiza munthu kukhala woleza mtima ndipo munthu akamaleza mtima amasonyeza kuti amakonda Mulungu komanso anthu ena. Munthu akamaleza mtima, chikondi chake chimalimba koma akamalephera kuchita zimenezi chikondi chake chimachepa ndipo anthu ena samukondanso. (1 Akor. 13:4; Agal. 5:22) Kuti munthu akhale woleza mtima ayenera kukhalanso ndi makhalidwe ena abwino. Mwachitsanzo, ayenera kukhala wopirira chifukwa khalidweli limamuthandiza kukhalabe ndi maganizo abwino akakumana ndi mavuto. (Akol. 1:11; Yak. 1:3, 4) Munthu woleza mtima amapewa kubwezera akalakwiridwa komanso amakhalabe wokhulupirika zivute zitani. Baibulo limanena kuti tiyenera kukhala ndi mtima wotha kudikira ndipo lemba la Yakobo 5:7, 8 limatsindika mfundo imeneyi. w17.08 4 ¶4

Lamlungu, December 22

Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.​—Yes. 41:10.

Achinyamata akhoza kuvomereza kuti munthu asanayambe ulendo amafunika kudziwiratu kumene akupita. Moyo wathuwu uli ngati ulendo ndipo ndi bwino kuti munthu azidziwiratu zimene adzachite pa moyo wake adakali wachinyamata. N’zoona kuti kusankha zochita pa moyo n’kovuta. Koma musataye mtima. Kumbukirani zimene Yehova ananena mulemba lalero. Yehova amatilimbikitsa kuti tizisankha zinthu mwanzeru. (Mlal. 12:1; Mat. 6:20) Iye amafuna kuti tizikhala osangalala. Umboni wa zimenezi ndi zinthu zosangalatsa zimene timadya, kumva kapena kuona m’chilengedwechi. Yehova amatisamaliranso ndipo amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tikhale osangalala. Anthu amene amakana malangizo ake, iye amawauza kuti: “Munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo. . . . Atumiki anga adzasangalala, koma inuyo mudzachita manyazi. Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.” (Yes. 65:12-14) Yehova amalemekezeka anthu ake akamasankha zochita mwanzeru.​—Miy. 27:11. w17.07 22 ¶1-2

Lolemba, December 23

[Yehova] amazitchula [nyenyezi zonse] mayina ake.—Sal. 147:4.

Ngati Yehova amadziwa pamene pali nyenyezi iliyonse pa nthawi ina iliyonse ndiye kuti amadziwanso za munthu aliyense payekha. Izi zikutanthauza kuti amadziwa kumene muli, mmene mukumvera mumtima mwanu komanso chimene mukufunikira pa nthawi ina iliyonse. Sikuti Yehova amangodziwa bwino za inuyo panokha. Iye ndi wamphamvu komanso wachifundo moti angathe kukuthandizani pa vuto lanu lililonse. (Sal. 147:5) Mwina nthawi zina mumaganiza kuti mavuto anu ndi aakulu kwambiri moti simungathe kuwapirira. Koma Yehova ndi wanzeru ndipo amadziwa zimene simungakwanitse komanso ‘amakumbukira kuti ndinu fumbi.’ (Sal. 103:14) Popeza si ife angwiro, timalakwitsa zinthu nthawi ndi nthawi. Timadandaula pamene talankhula mawu olakwika, kuchita zinthu zolakwika kapena kusirira zimene anthu ena ali nazo. Yehova alibe mavuto ngati amenewa koma amatimvetsa bwino kwambiri. (Yes. 40:28) Mwina inuyo panokha mwaona Yehova akukuthandizani pa vuto linalake.​—Yes. 41:10, 13. w17.07 18-19 ¶6-8

Lachiwiri, December 24

Wa diso labwino [kapena kuti wowolowa manja] adzadalitsidwa.—Miy. 22:9.

M’bale wina wa ku Sri Lanka atasamukira kudziko lina, anapereka malo ake kuti anthu azichitirapo misonkhano yampingo ndi ikuluikulu komanso kuti kuzigona atumiki a nthawi zonse. M’baleyu analolera kuchita zimenezi kuti athandize abale ndi alongo ovutika a m’dzikoli. M’mayiko ena amene ntchito yathu ndi yoletsedwa, abale ndi alongo amalola kuti anthu azisonkhana m’nyumba zawo. Izi zimathandiza kuti apainiya komanso abale ena ovutika apeze malo ochitira misonkhano popanda kulipira ndalama. Mlongo wina amene amakonda kupereka ndalama zothandizira pa ntchito za Ufumu anafotokoza mmene Mulungu wamudalitsira. Iye anati: “Ndimaona kuti kukhala ndi mtima wopatsa kumandithandiza kwambiri. Ndikamapatsa anthu zinthu zambiri, mtima wofuna kusonyeza chikondi kwa anthu umakulanso kwambiri. Ndimaona kuti ndimayambanso kukhala wokhululuka kwambiri, woleza mtima komanso sinditaya mtima ndikakhumudwitsidwa kapena kupatsidwa malangizo.” w17.07 9 ¶9-10

Lachitatu, December 25

Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chikhale m’manja mwako.”​—Yobu 1:12.

Ngakhale atakhala kuti anamvetsa zimene zinachititsa mavuto akewo, ayenera kuti nthawi zina ankadzifunsa kuti, ‘Kodi zinalidi zofunika kuti mavuto ake afike poipa kwambiri choncho?’ Kaya ankaganiza zotani, kuganizira malangizo amene Mulungu anamupatsa kukanamuthandiza. Ndipo izi zikanachititsa kuti akhale ndi maganizo oyenera komanso kuti alimbikitsidwe. (Sal. 94:19) Nkhani ya Yobu ikhozanso kutilimbikitsa komanso kutithandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera. Ndipo Yehova analola kuti nkhaniyi isungidwe m’Mawu ake ‘kuti itilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.’ (Aroma 15:4) Ndiye kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yobuyi? Phunziro lalikulu ndi lakuti tisalole kuti zimene zikuchitika pa moyo wathu zitiiwalitse mfundo yakuti nkhani yofunika kwambiri ndi ya ulamuliro wa Yehova. Tizikumbukiranso kuti tikamatsanzira Yobu, n’kumakhala okhulupirika ngakhale pa nthawi imene tikuvutika kwambiri, tidzasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Mulungu. w17.06 24 ¶9; 25 ¶13-14

Lachinayi, December 26

Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.​—Maliko 6:31.

Yesu anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Tsiku lina atalalikira kwa nthawi yaitali, anauza ophunzira ake mawu amene ali pamwambawa. Kupeza nthawi yopuma komanso yosangalala kumatithandiza. Koma pamakhala mavuto ngati munthu amangoganizira zosangalala basi. M’nthawi ya atumwi, anthu ambiri ankayendera mfundo yoti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akor. 15:32) Masiku anonso, anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa.Koma kodi tingadziwe bwanji ngati tili ndi maganizo oyenera pa nkhani ya zosangalatsa? Tingachite bwino kuona zimene tachita mlungu umenewo. Kodi ndi maola angati amene tachita zinthu zokhudza kulambira? Nanga ndi maola angati amene timangocheza, kuchita masewera enaake kapena kuonera TV? Kodi taona kuti tikufunikira kusintha zinthu zina?​—Aefeso 5:15, 16. w17.05 24-25 ¶11-13

Lachisanu, December 27

Ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino.—Mat. 13:45.

Mufanizo la Yesuli, wamalondayo anapeza ngale yamtengo wapatali kwambiri. Koma kuti agule ngaleyo analolera kugulitsa zonse zimene anali nazo. Apa n’zoonekeratu kuti munthuyo ankaona kuti ngaleyo inali yamtengo wapatali kwambiri. Ufumu wa Mulungu uli ngati ngale yamtengo wapatali. Tikamaukonda ngati mmene wamalonda uja ankakondera ngale ija, tidzalolera kusiya zonse zimene tili nazo n’cholinga choti tikhale nzika ya Ufumuwo. (Maliko 10:28-30) Mwachitsanzo, Zakeyu anapeza chuma chambiri chifukwa chobera anthu. (Luka 19:1-9) Komabe atamva Yesu akulalikira za Ufumu, anazindikira kufunika kwa zimene anamvazo ndipo nthawi yomweyo anasintha. Iye ananena kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu ndibweza kuwirikiza kanayi.” Zakeyu anagawadi chuma chimene anachipeza mwachinyengo ndipo anasiya mtima wadyera. w17.06 10 ¶3-5

Loweruka, December 28

Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.​—3 Yoh. 4.

Anthu amene apemphedwa ndi makolo kuti azithandiza ana awo ayenera kunena zinthu zabwino zokhudza makolowo akamalankhula ndi anawo. Izi zingathandize kuti anawo azilemekeza makolo awo. Komanso anthuwo sayenera kuona kuti apatsidwa udindo wa makolowo. Iwo ayeneranso kupewa kuchita zinthu zomwe zingapangitse anthu amumpingo kapena amene si Mboni kukayikira zolinga zawo. (1 Pet. 2:12) Nawonso makolowo sayenera kungosiyira anthu enawo udindo wophunzitsa ana awo za Yehova. M’malomwake ayenera kuchita chidwi ndi zimene anthuwo akuchita ndi ana awo komanso ayenera kupitiriza kuwaphunzitsa okha. Ngati ndinu makolo, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni komanso kuchita zonse zimene mungathe pophunzitsa ana anu. (2 Mbiri 15:7) Muziona kuti udindo wothandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa zofuna zanu. Muziyesetsa kwambiri kuti mufike ana anu pamtima ndi Mawu a Mulungu. Musamakayikire kuti mwana wanu akhoza kukhala mtumiki wokhulupirika wa Yehova. w17.05 12 ¶19-20

Lamlungu, December 29

Sindingachite zimenezo pamaso pa Yehova, kupereka cholowa cha makolo anga kwa inuyo.​—1 Maf. 21:3.

Bambo wina ananamiziridwa kuti wapalamula mlandu waukulu. Achibale ake komanso anzake anadabwa kuona kuti bamboyo waweruzidwa kuti aphedwe ngakhale kuti anthu amene anapereka umboni anali osadalirika. Anthu okonda chilungamo zinawapweteka kwambiri kuona bambo wosalakwayo limodzi ndi ana ake aamuna akuphedwa. Zimene tafotokozazi zinachitikira mtumiki wa Yehova wokhulupirika dzina lake Naboti. Iye anaphedwa limodzi ndi ana ake mu ulamuliro wa Mfumu Ahabu ya Isiraeli. (1 Maf. 21:11-13; 2 Maf. 9:26) Pa nthawi ina Mfumu Ahabu anauza Naboti kuti amugulitse munda wake wa mpesa kapena asinthane ndi wina. Koma Naboti anakana. Kodi n’chifukwa chiyani anakana? Naboti anakana zimene Ahabu ankafunazo chifukwa choti ankatsatira lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Lamulo lake linali lakuti munthu asamagulitse mpaka kalekale cholowa cha fuko lawo. (Lev.25:23; Num. 36:7) Izi zikusonyeza kuti Naboti anali ndi maganizo a Yehova pa nkhaniyi. w17.04 23 ¶1; 24 ¶4

Lolemba, December 30

Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.​—Sal. 37:10.

Ndani adzalowe m’malo mwa anthu oipa? Yehova anatilonjeza kuti: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Baibulo limanenanso kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29) Kodi “ofatsa” komanso “olungama” amene atchulidwa m’mavesiwa ndi ndani? Ofatsa ndi anthu odzichepetsa amene amalola kuti Yehova aziwaphunzitsa komanso kuwatsogolera. Olungama ndi anthu amene amakonda kuchita zinthu zimene Yehova amaona kuti ndi zolungama. Masiku ano anthu ofatsa komanso olungama ndi ochepa kwambiri poyerekezera ndi anthu oipa. Koma m’dziko latsopano mudzakhala anthu olungama okhaokha. Anthu amenewa ndi amene adzathandize kuti dzikoli likhalenso Paradaiso. w17.04 10-11 ¶5-6

Lachiwiri, December 31

Usalephere kuchitira zabwino anthu . . . pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.​—Miy. 3:27.

Chifukwa chokonda Mulungu, timasonyezana chikondi makamaka pa nthawi ya mavuto. (1 Yoh. 3:17, 18) Mwachitsanzo, pamene Akhristu a ku Yuda ankavutika ndi njala, mpingo unakonza zoti alandire thandizo. (Mac. 11:28, 29) Mtumwi Paulo komanso Petulo analimbikitsanso Akhristu kuti azikhala ochereza. (Aroma 12:13; 1 Pet. 4:9) Ngati timafunika kulandira Akhristu anzathu amene angobwera kudzacheza, kuli bwanji amene athawa kwawo chifukwa choti moyo wawo unali pa ngozi kapena akuzunzidwa chifukwa chokhala a Mboni? Posachedwapa, a Mboni za Yehova ambirimbiri anathawa nkhondo imene inkachitika m’madera akum’mawa m’dziko la Ukraine. Mwatsoka, ena mwa iwo anaphedwa. Koma ambiri anatha kuthawa ndipo abale ndi alongo a m’madera ena a ku Ukraine ndiponso a m’dziko la Russia anawalandira m’nyumba zawo. A Mboni a m’mayiko onse awiriwa akupewabe kukhala “mbali ya dziko” ndipo akupitiriza mwakhama ‘kulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.’​—Yoh. 15:19; Mac. 8:4. w17.05 4 ¶6-7

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena