Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 108-118
  • November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Lachisanu, November 1
  • Loweruka, November 2
  • Lamlungu, November 3
  • Lolemba, November 4
  • Lachiwiri, November 5
  • Lachitatu, November 6
  • Lachinayi, November 7
  • Lachisanu, November 8
  • Loweruka, November 9
  • Lamlungu, November 10
  • Lolemba, November 11
  • Lachiwiri, November 12
  • Lachitatu, November 13
  • Lachinayi, November 14
  • Lachisanu, November 15
  • Loweruka, November 16
  • Lamlungu, November 17
  • Lolemba, November 18
  • Lachiwiri, November 19
  • Lachitatu, November 20
  • Lachinayi, November 21
  • Lachisanu, November 22
  • Loweruka, November 23
  • Lamlungu, November 24
  • Lolemba, November 25
  • Lachiwiri, November 26
  • Lachitatu, November 27
  • Lachinayi, November 28
  • Lachisanu, November 29
  • Loweruka, November 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 108-118

November

Lachisanu, November 1

[Muzikana] moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma [muzikhala] amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu.​—Tito 2:12.

Munthu amene amadziletsa amayesetsa kuti asachite zinthu zolakwika komanso asinthe khalidwe ndi maganizo ake. Koma kudziletsa si khalidwe limene timabadwa nalo. Munthu amachita kuphunzira.Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo nthawi zonse komanso moleza mtima ndi kuwalera “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ana amafunika kuwathandiza kuti azitha kudziletsa n’cholinga choti akhale anzeru. Mfundo zimene takambiranazi zimagwiranso ntchito kwa anthu amene aphunzira za Yehova atakula kale. N’zoona kuti amakhala atayamba kudziletsa pa zinthu zina. Komabe mwauzimu tinganene kuti amakhalabe ana. Koma pang’ono ndi pang’ono akhoza kukula n’kumakhala ndi makhalidwe a Khristu. Apa zimakhala ngati akuvala “umunthu watsopano.” (Aef. 4:23, 24) Kuti avale umunthu watsopanowu ayenera kukhala odziletsa. w18.03 29 ¶3-4

Loweruka, November 2

Khalani ochereza.​—Aroma 12:13.

Munthu aliyense yemwe wafika pamisonkhano amabwera kuti adzalandire chakudya chauzimu. Choncho tonse timakhala ngati alendo amene aitanidwa ndi Yehova komanso gulu lake. (Aroma 15:7) Koma anthu atsopano akafika, amakhalanso ngati alendo athu. Ndiye tiyenera kuwalandira bwino mosaganizira za mmene akuonekera kapena mmene avalira. (Yak. 2:1-4) Ngati munthu wina wangobwera popanda winawake amene wamuitana, ndi bwino kumupempha kuti tikhale naye pamodzi. Mwina tingamuthandize kuti azitsatira bwinobwino nkhani zimene zikukambidwa komanso kuti aziona nawo Malemba. Tikatero tidzakhala tikutsatira malangizo akuti: “Khalani ochereza.” Timakhalanso ndi mwayi wochereza alendo pa nthawi imene abale ochokera m’mipingo ina abwera kudzakamba nkhani, kukabwera oyang’anira madera kapena abale ochokera ku ofesi ya nthambi. (3 Yoh. 5-8) Mwachitsanzo, tikhoza kuwaitanira zakudya kapena zakumwa. Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuchereza? w18.03 15 ¶5, 7

Lamlungu, November 3

Chikundiletsa kubatizidwa n’chiyani?​—Mac. 8:36.

Taganizirani chitsanzo cha Saulo amene poyamba anali wodzipereka kwambiri pa miyambo yachiyuda ndipo ankazunza Akhristu. Iye anabadwira mu mtundu wa Ayuda womwe unadzipereka kwa Mulungu. Koma pa nthawiyi Ayudawo anali atasokoneza ubwenzi wawo wapadera ndi Yehova. Ndiyeno Yesu Khristu, yemwe panthawiyo anali atabwerera kumwamba, anaonekera kwa Saulo. Ndiye kodi Sauloyo anatani? Iye anavomera kuti athandizidwe ndi Mkhristu wina dzina lake Hananiya. Baibulo limanena kuti atangothandizidwa “anapita kukabatizidwa.” (Mac. 9:17, 18; Agal. 1:14) Kenako anayamba kutchedwa kuti mtumwi Paulo. Kodi mwaona kuti Paulo atangozindikira za udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu anabatizidwa popanda kuzengereza? (Mac. 22:12-16) Masiku anonso, ophunzira Baibulo ambiri amachita zimenezi, kaya akhale achikulire kapena achinyamata. w18.03 5-6 ¶9-11

Lolemba, November 4

Sindinathe kulankhula nanu monga anthu auzimu, koma monga anthu oganiza ngati anthu a m’dzikoli.​—1 Akor. 3:1.

Yakobo ankakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, ankafunika kupirira zochita za mkulu wake yemwe ankafunanso kumupha. Apongozi akenso anamuchitira zinthu zachinyengo kambirimbiri. Koma ngakhale kuti ankakhala ndi anthu okonda za m’dziko, Yakobo anakhalabe munthu wauzimu. (1 Akor. 2:14-16) Iye ankakhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza Abulahamu ndipo ankayesetsa kusamalira bwino banja lake podziwa kuti lidzathandiza pokwaniritsa cholinga cha Yehova. (Gen. 28:10-15) Zolankhula komanso zochita za Yakobo zinkasonyeza kuti ankaganizira mfundo za Mulungu komanso cholinga chake. Mwachitsanzo, pa nthawi imene ankaopa kuphedwa ndi Esau, iye anapempha Mulungu kuti: “Ndapota nanu, ndipulumutseni . . . Inuyotu munanena kuti, ‘Mosakayikira m’pang’ono pomwe ndidzakusamalira, ndipo ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa kunyanja.’” (Gen. 32:6-12) Apa zikuonekeratu kuti Yakobo ankakhulupirira kwambiri zimene Yehova analonjeza ndipo ankachita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulunguyo. w18.02 20 ¶9-10

Lachiwiri, November 5

Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.—Yobu 1:8.

Zinthu zambiri zinasintha pa moyo wa Yobu. Iye asanakumane ndi mayesero ake, anali “munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kum’mawa.” (Yobu 1:3) Yobu anali wolemera, wotchuka komanso anthu ambiri ankamulemekeza. (Yobu 29:7-16) Ngakhale zinali choncho, sankadziona kuti ndi wapamwamba kwambiri kapena kuona kuti sakufunikira thandizo la Mulungu. Ndipotu Yehova anatchula Yobu kuti “mtumiki wanga.” Satana anabweretsera Yobu mavuto osiyanasiyana moti Yobu ankaganiza kuti mavutowo akuchokera kwa Yehova. (Yobu 1:13-21) Kenako anthu atatu omwe ankangonamizira kuti ndi anzake anabwera kudzamuona ndipo analankhula mawu opweteka kwambiri. Ananena zinthu zosonyeza kuti Mulungu akumulanga chifukwa cha zimene analakwitsa. (Yobu 2:11; 22:1, 5-10) Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika. N’zoona kuti nthawi zina analankhula mosaganiza koma Yehova anamvetsa mmene ankamvera mumtima mwake. (Yobu 6:1-3) Mulungu anazindikira kuti Yobu anakhumudwa kwambiri koma anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti Satana anamuzunza koopsa komanso kumunamizira. Mayeserowo atatha, Yehova anamubwezera zinthu zake kuwirikiza kawiri pa zimene anali nazo poyamba ndipo anakhalanso moyo zaka zina 140. (Yak. 5:11) Pa zaka zimenezinso, Yobu anapitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse. w18.02 6 ¶16; 7 ¶18

Lachitatu, November 6

Anthu adzakhala . . . odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada.​—2 Tim. 3:2, 4.

Anthu amakhalidwe amenewa amalakalaka kuti ena aziwatama kapena kuwasirira. Katswiri wina analemba kuti munthu wonyada kwambiri amadziona kuti ndi wapadera moti tingati amadzilambira yekha. Anthu ena amanena kuti khalidwe lonyada ndi lonyansa kwambiri moti ngakhale anthu onyadawo amanyansidwa ndi anthu ena amene ali ndi khalidweli. Yehova amadana ndi khalidwe la kunyada. Paja Baibulo limanena kuti iye amanyansidwa ndi “maso odzikweza.” (Miy. 6:16, 17) Munthu wonyada sangakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Sal. 10:4) Mdyerekezi ndi wonyada. (1 Tim. 3:6) Koma n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale atumiki ena a Yehova anayamba kusonyeza khalidweli. Mwachitsanzo Uziya, yemwe anali mfumu ya ku Yuda, anakhala wokhulupirika kwa zaka zambiri, koma Baibulo limanena kuti: “Atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa. Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.” Pa nthawi ina, nayenso Mfumu Hezekiya anayamba mtima wonyada koma kenako anasiya.​—2 Mbiri 26:16; 32:25, 26. w18.01 28 ¶4-5

Lachinayi, November 7

Aliyense aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake?​—1 Akor. 16:2.

M’Malemba muli zitsanzo zambiri za anthu amene anapereka zinthu zawo kwa Yehova. Nthawi zina anthu a Yehova ankapereka zinthu pofuna kuthandiza pa ntchito zapadera. (Eks. 35:5; 2 Maf. 12:4, 5; 1 Mbiri 29:5-9) Nawonso Akhristu oyambirira atamva kuti abale awo akuvutika ndi njala, “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.” (Mac. 11:27-30) Koma zinthu zimene anthuwo ankapereka ankazipeza m’njira zosiyanasiyana. Mu nthawi ya atumwi, Akhristu ena ankagulitsa chuma chawo, monga minda ndi nyumba, ndipo ankabweretsa ndalama zimene anapezazo kwa atumwi. Ndiyeno atumwiwo ankapereka ndalamazo kwa anthu ena kuti ziwathandize. (Mac. 4:34, 35) Koma Akhristu ena ankaika ndalama zinazake pambali n’cholinga choti azipereka pothandiza pa ntchito ya Mulungu. Choncho anthu onse, kaya olemera kapena osauka, ankatha kupereka zinthu zawo.​—Luka 21:1-4. w18.01 18 ¶7; 19 ¶9

Lachisanu, November 8

Anyamata adzatopa n’kufooka.—Yes. 40:30.

Tonsefe, kaya tili ndi maluso otani, pali zinthu zina zimene sitingakwanitse patokha. Aliyense ayenera kuzindikira mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, Paulo anali waluso kwambiri, koma panali zinthu zina zimene sankakwanitsa kuchita. Iye atauza Mulungu nkhawa zake, Mulunguyo anamuuza kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.” Paulo anamvetsa zimenezi ndipo anati: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.” (2 Akor. 12:7-10) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye anazindikira kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita popanda kuthandizidwa ndi Mulungu. Choncho mzimu wa Mulungu unkamupatsa mphamvu pamene ankafooka komanso kuti achite zinthu zimene payekha sakanakwanitsa. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Mulungu akhozanso kutipatsa mphamvu zambiri. w18.01 9 ¶8-9

Loweruka, November 9

Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke.—2 Tim. 3:15.

Ngati mwana wanena kuti akufuna kubatizidwa, makolo ayenera kufufuza kaye zinthu zothandiza pophunzitsa ana zimene gulu la Yehova lapereka. Akatero adzatha kuthandiza mwanayo kuti amvetse zoti munthu akadzipereka kwa Mulungu n’kukhala Mkhristu amakhala ndi udindo waukulu koma amapezanso madalitso ambiri. Makolo ali ndi mwayi komanso udindo waukulu wolera ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Izi zingatheke ngati makolowo amaphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo komanso kuwathandiza kuti azizikhulupirira kwambiri. Chikhulupiriro chawo chiyenera kukhala champhamvu moti chingawalimbikitse kudzipereka kwa Yehova n’kumamutumikira ndi mtima wonse. Tikukhulupirira kuti Mawu a Yehova, mzimu wake komanso khama lanu zidzathandiza kuti ana anu apeze ‘nzeru zowathandiza kuti adzapulumuke.’ w17.12 22 ¶17, 19

Lamlungu, November 10

Udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.​—Dan. 12:13.

Danieli anali wachikulire kwambiri, wazaka pafupifupi 100. Kodi Danieli anali m’gulu la anthu amene adzauke? Inde. Tikutero chifukwa chakuti chakumapeto kwa buku la Danieli timawerenga mawu olimbikitsa amene Mulungu anamuuza akuti: “Ndiyeno iwe pita ku mapeto ndipo udzapuma.” (Dan. 12:13) Danieli anazindikira kuti akufa amakhala ngati akupumula ndipo kumanda kumene ankapita kulibe “kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru.” (Mlal. 9:10) Koma amenewa sanali mapeto a zonse. Uthenga umene Mulungu anauza Danieli unapitiriza ndi mawu amulemba la leroli. Danieli sanauzidwe za tsiku kapena nthawi. Anangouzidwa kuti akadzafa zidzakhala ngati wapita kumapeto n’kupuma. Koma mawu oti “udzauka kuti ulandire gawo lako” anamutsimikizira kuti akadzafa, adzauka patapita nthawi yaitali. Nthawi imene adzaukeyo ndi imene anaifotokoza kuti “pa mapeto a masikuwo.” Baibulo lina linamasulira mawu amene Danieli anauzidwawa kuti: “Udzauka kuti ulandire gawo lako pa nthawi ya mapeto.”​—Jerusalem Bible. w17.12 7 ¶17-18

Lolemba, November 11

Umboni wa munthu mmodzi si wokwanira kuti munthu aphedwe.​—Num. 35:30.

Yehova anauza akulu a ku Isiraeli kuti azitsatira mfundo zake zachilungamo poweruza milandu. Choyamba, ankafunika kumvetsa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. Kenako ankafunika kuganizira cholinga cha munthu amene wapha mnzake, mtima wake komanso zimene wakhala akuchita. Kuti asonyeze chilungamo cha Mulungu, ankafunika kuona ngati munthuyo anapha mnzake “chifukwa chodana naye” kapena “kuchita kum’bisalira.” (Num. 35:20-24) Popereka umboni wotsimikizira kuti munthuyo anapha mnzake mwadala, umboni wake unkayenera kukhala wa anthu awiri kapena kuposerapo. Choncho pambuyo pofufuza zimene zinachitika, akulu ankafunika kuganizira munthuyo osati kungoganizira zimene zinachitika. Ankafunika kukhala ozindikira kuti athe kuona nkhani yonseyo bwinobwino, osati kungoiona pamwambamwamba. Koma kuposa zonse, ankafunika kuthandizidwa ndi mzimu woyera kuti athe kutsanzira Yehova posonyeza chifundo, chilungamo komanso kuzindikira.​—Eks. 34:6, 7. w17.11 16 ¶13-14

Lachiwiri, November 12

Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama.​—1 Tim. 4:15.

Titangoyamba kuphunzira Mawu a Mulungu tinapeza mfundo zina zamtengo wapatali. Tinganene kuti mfundozi ndi “zakale” chifukwa takhala tikuzidziwa kuchokera pamene tinayamba choonadi. Kodi mfundo zina zimene tinaphunzira ndi ziti? Tinaphunzira kuti Yehova ndi amene anatilenga ndipo ali nafe cholinga. Tinaphunziranso kuti Mulungu amatikonda kwambiri moti anapereka nsembe ya dipo ya Mwana wake n’cholinga choti timasuke ku uchimo ndi imfa. Komanso tinaphunzira kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto athu onse ndipo tidzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’dziko lamtendere. (Yoh. 3:16; Chiv. 4:11; 21:3, 4) Nthawi zina kafotokozedwe ka mfundo zina za m’Baibulo kakhoza kusintha. Izi zikachitika tiyenera kuphunzira mfundozi mosamala komanso kuziganizira kwambiri. (Mac. 17:11) Zimenezi zingatithandize kumvetsa bwino mfundo zikuluzikulu komanso zing’onozing’ono zimene zasintha. Tikamatero timakhala kuti tikusunga bwinobwino mfundozi mosungiramo chuma chathu. w17.06 12-13 ¶15-16

Lachitatu, November 13

Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa [ndi] chilakolako cha kugonana.​—Akol. 3:5.

Tiyenera kusamala kwambiri tikakumana ndi zinthu zimene zingatichititse kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za Yehova. Mwachitsanzo, anthu akakhala pa chibwenzi angachite bwino kuikiratu malire pa zinthu monga kugwirana, kukisana kapena kukhala awiriwiri. (Miy. 22:3) Mkhristu akhoza kukumananso ndi zinthu zimene zingamugwetsere mumsampha akapita kukagwira ntchito kutali kapena akamagwira ntchito ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake. (Miy. 2:10-12, 16) Pamene tikuda nkhawa kapena kusowa wocheza naye m’pamene tiyenera kusamala kwambiri. Zili choncho chifukwa chakuti pa nthawi imeneyi m’pamene timafunitsitsa kuti munthu wina atichezetse ndipo tikhoza kulolera kuchezetsedwa ndi aliyense amene angapezeke. Choncho ngati muli ndi nkhawa kapena mukusowa wocheza naye, muyenera kudalira Yehova komanso anthu ake.​—Sal. 34:18; Miy. 13:20. w17.11 26 ¶4-5

Lachinayi, November 14

Sankhani mizinda yothawirako.—Yos. 20:2.

Yehova amaona kuti kupha munthu ndi mlandu waukulu kwambiri. Pa nthawi ya Aisiraeli, munthu akapha mnzake mwadala nayenso ankaphedwa ndi wachibale wamwamuna wa wophedwayo. Wachibaleyo ankadziwika kuti “Wobwezera magazi.” (Num. 35:19) Kupha munthu wolakwayo kunkathandiza kuti mlandu wopha munthu wosalakwa uphimbidwe. Kuchita zimenezi mwamsanga kunkathandiza kuti Dziko Lolonjezedwa lisaipitsidwe, chifukwa Yehova analamula kuti: ‘Musadetse dziko limene mukukhalamo, chifukwa kukhetsa magazi a anthu n’kumene kumadetsa dziko.’ (Num. 35:33, 34) Koma kodi Aisiraeli ankatani ngati munthu wapha mnzake mwangozi? Ngakhale munthu atachita zimenezo mwangozi, ankakhalabe ndi mlandu wopha munthu wosalakwa. (Gen. 9:5) Koma ankachitiridwa chifundo ndipo ankaloledwa kuti athawire kumzinda wothawirako kuti wobwezera magazi asamuphe. Akafika mumzindawo ankakhala wotetezeka ndipo ankafunika kukhalabe mumzindawo mpaka mkulu wa ansembe atafa.​—Num. 35:15, 28. w17.11 9 ¶3-5

Lachisanu, November 15

Wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.​—Miy. 12:16.

Mlongo wina wa ku Australia anati: “Apongozi anga aamuna ankatsutsa kwambiri choonadi. Choncho tisanawaimbire foni kuti tione ngati ali bwino, ine ndi mwamuna wanga tinkapempha Yehova kuti atithandize n’cholinga choti tisakhumudwe akatikwiyira. Sitinkalankhula nawo kwa nthawi yaitali poopa kuti tingayambe kukambirana kwambiri nkhani zachipembedzo zimene zingayambitse mikangano.” Tikasiyana maganizo ndi achibale athu tikhoza kudziimba mlandu makamaka chifukwa chakuti timawakonda ndipo sitifuna kuwakhumudwitsa. Komabe tizikumbukira kuti kusangalatsa Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kusangalatsa achibale athu. Zimenezi zingathandize achibalewo kuzindikira kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo ndi nkhani yaikulu yomwe ingachititse kuti munthu adzapeze moyo kapena ayi. Kaya zinthu zili bwanji, tizikumbukira kuti sitingakakamize munthu kuti ayambe kuphunzira choonadi. M’malomwake tizingoyesetsa kuchita zinthu zimene zingawathandize kuona ubwino wotsatira mfundo za Yehova. Yehova amapereka kwa munthu aliyense ufulu wosankha kumutumikira kapena ayi.​—Yes. 48:17, 18. w17.10 15-16 ¶15-16

Loweruka, November 16

Tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18.

Sitiyenera kusonyeza chikondi ndi mawu okha pa nthawi imene tikufunikira kuchisonyeza ndi zochita zathu. Mwachitsanzo, ngati Mkhristu mnzathu akusowa zofunika pa moyo, tiyenera kumuthandiza osati kungomuuza kuti tikumufunira zabwino zonse. (Yak. 2:15, 16) Chifukwa chokonda Yehova ndi anzathu, timayesetsanso kuchita zambiri pa ntchito yolalikira, osati kungopempha Mulungu kuti “atumize antchito” ambiri oti azigwira ntchitoyi. (Mat. 9:38) Mtumwi Yohane analemba kuti tiyenera kusonyeza “chikondi chenicheni m’zochita zathu.” Choncho chikondi chathu sichiyenera kukhala “cha chiphamaso” kapena ‘chachinyengo.’ (Aroma 12:9; 2 Akor. 6:6) Zimenezi zikutanthauza kuti n’zosatheka kunamizira kuti tili ndi chikondi chenicheni. Munthu amene amasonyeza chikondi chachinyengo sitinganene kuti ndi wachikondi. w17.10 8 ¶5-6

Lamlungu, November 17

Uziliwerenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, . . . ndipo udzachita zinthu mwanzeru.​—Yos. 1:8.

Kuti Mawu a Mulungu azitithandiza tiyenera kuwawerenga tsiku lililonse ngati n’zotheka. N’zoona kuti ambirife timatanganidwa kwambiri. Komabe sitiyenera kulola chilichonse, ngakhale chimene tikuona kuti n’chofunika, kuti chitilepheretse kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Aef. 5:15, 16) Atumiki ambiri a Yehova amayesetsa kupeza nthawi yoti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse. Ena amaliwerenga m’mawa pomwe ena amachita zimenezi asanakagone. Iwo amakhala ndi maganizo ofanana ndi a wolemba masalimo amene ananena kuti: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.” (Sal. 119:97) Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo tiyeneranso kusinkhasinkha zimene tawerengazo. (Sal. 1:1-3) Tikamachita zimenezi tidzatha kugwiritsa ntchito bwino nzeru za Mulungu pa moyo wathu. Kaya timagwiritsa ntchito Baibulo lenileni kapena timaliwerenga pachipangizo chamakono, tiyenera kukhala ndi cholinga choti mawuwo azitifika pamtima. w17.09 24 ¶4-5

Lolemba, November 18

Nonsenu mukhale . . . achifundo chachikulu.​—1 Pet. 3:8.

Sikuti chifundo chiyenera kusonyezedwa pa nthawi ina iliyonse. Mwachitsanzo, zimene Sauli anachita poganiza kuti n’chifundo zinali zolakwika. Iye sanamvere Mulungu chifukwa sanaphe Agagi, yemwe anali mdani wa anthu a Mulungu. Izi zinachititsa kuti Yehova aone kuti Sauli si woyeneranso kukhala mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 15:3, 9, 15) Yehova ndi woweruza wabwino chifukwa amaona zimene zili mumtima wa munthu ndipo amadziwa ngati ndi woyenera kuchitiridwa chifundo kapena ayi. (Maliro 2:17; Ezek. 5:11) Posachedwapa, iye adzawononga anthu onse amene samumvera. (2 Ates. 1:6-10) Pa nthawiyo, iye sadzachitira chifundo anthu amene wawaweruza kuti akuyenera kuphedwa. Koma adzapha anthu oipawo pofuna kusonyeza chifundo kwa anthu olungama amene adzapulumuke. Si udindo wathu kuweruza anthu kuti akuyenera kuphedwa kapena kukhala ndi moyo. M’malomwake, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize. w17.09 10-11 ¶10-12

Lachiwiri, November 19

Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo . . . kudziletsa.​—Agal. 5:22, 23.

Kudziletsa ndi limodzi mwa makhalidwe amene Mulungu ali nawo. Yehova amatha kusonyeza bwino kwambiri khalidwe limeneli. Koma anthufe zimativuta kudziletsa chifukwa si ife angwiro. Zimenezi zimachititsa kuti tizikumana ndi mavuto ambiri. Munthu amene sadziletsa angamavutike kuchita zinthu pa nthawi yake, kugwira bwino ntchito komanso kukhoza bwino kusukulu. Mwina angachitenso zinthu monga kulalatira ena, kuledzera, kuchita chiwawa, kutenga ngongole yosafunika ndiponso kuthetsa banja. Angakumanenso ndi mavuto monga kuvutika maganizo, matenda opatsirana pogonana, mimba yapathengo komanso kumangidwa. (Sal. 34:11-14) Apa zikuonekeratu kuti anthu amene sadziletsa amakumana ndi mavuto komanso amabweretsera anzawo mavuto. Vuto la kusadziletsa lafala kwambiri masiku ano. M’ma 1940, anthu anachita kafukufuku yemwe anasonyeza kuti anthu amavutika kudziletsa. Koma kafukufuku wina amene wachitika posachedwapa amasonyeza kuti masiku ano zinthu zafika poipa kwambiri pa nkhaniyi. Mfundo imeneyi ndi yosadabwitsa kwa anthu amene amadziwa Baibulo chifukwa linaneneratu kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala “osadziletsa.”​—2 Tim. 3:1-3. w17.09 3 ¶1-2

Lachitatu, November 20

Mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.​—Afil. 4:7.

Tikakhala ndi “mtendere wa Mulungu” mitima yathu ndi maganizo athu zimakhala m’malo. Timadziwa kuti Yehova amatikonda ndipo amatifunira zabwino. (1 Pet. 5:10) Kudziwa zimenezi kumatiteteza kuti tisamapanikizike ndi nkhawa komanso tisamakhumudwe kwambiri. Posachedwapa, padzikoli pachitika chisautso chachikulu kuposa chilichonse chimene chinachitikapo. (Mat. 24:21, 22) Panopa sitikudziwa zimene aliyense wa ife angakumane nazo pa nthawiyo. Koma palibe chifukwa choti tizidera nkhawa kwambiri. Ngakhale kuti sitidziwa zonse zimene Yehova adzachite, Yehovayo timamudziwa bwino. Zimene wakhala akuchita m’mbuyomu zimasonyeza kuti pa vuto lililonse, iye amatha kukwaniritsa cholinga chake ndipo nthawi zina amakwaniritsa m’njira imene anthu sankayembekezera. Nthawi iliyonse imene Yehova amatichitira zimenezi, tikhoza kuona njira yatsopano imene ‘mtendere wa Mulungu umaposera kuganiza mozama kulikonse.’ w17.08 12 ¶16-17

Lachinayi, November 21

Lezani mtima . . . kufikira kukhalapo kwa Ambuye.​—Yak. 5:7.

Mneneri Yesaya anafunsa kuti, “Mpaka liti?” ndipo mneneri Habakuku anafunsa kuti, “Kufikira liti?” (Yes. 6:11; Hab. 1:2) Nayenso Mfumu Davide, yemwe analemba Salimo 13, anafunsa maulendo 5 kuti: “Kufikira liti?” (Sal. 13:1, 2) Ngakhale Yesu Khristu Ambuye wathu anafunsa funso lomweli ataona anthu opanda chikhulupiriro. (Mat. 17:17) Choncho tisamadabwe ngati nthawi zina nafenso timadzifunsa funso limeneli. Koma kodi n’chiyani chingatichititse kufunsa kuti, “Mpaka liti”? Mwina anthu akhala akutichitira zinthu zopanda chilungamo. Apo ayi tikuvutika ndi ukalamba, matenda kapena mavuto ena a ‘munthawi yovutayi.’ (2 Tim. 3:1) Mwinanso tatopa ndi maganizo olakwika amene anthu ambiri ali nawo. Kaya vuto limene latitopetsa ndi lotani, n’zolimbikitsa kudziwa kuti atumiki a Yehova akale, omwe analinso okhulupirika, sanadzudzulidwe atafunsa funso lomweli. Kodi n’chiyani chingatithandize pa nthawi imene takumana ndi mavuto ngati amenewa? Yakobo anayankha funsoli mulemba lalero. w17.08 3-4 ¶1-3

Lachisanu, November 22

Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama.​—Luka 16:9.

Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti agwiritse ntchito “chuma chosalungama” kuti apeze mabwenzi kumwamba. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti ndife okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma chathu chosalungama ndi kupereka ndalama zothandizira pa ntchito imene Yesu ananeneratu kuti izichitika masiku ano. (Mat. 24:14) Mwachitsanzo, mtsikana wina wamng’ono wa ku India anali ndi kabokosi kamene ankaponyamo ndalama ndipo pena ankalolera kuti asakhale ndi zidole kuti achite zimenezi. Bokosilo litadzaza anapereka ndalamazo kuti zithandize pa ntchito yolalikira. Ku India komweko kuli m’bale wina amene ali ndi munda wa kokonati ndipo amapereka kokonati wambiri ku ofesi ina ya omasulira mabuku. Iye atazindikira kuti abale a ku ofesiyo amagula kokonati, anaona kuti kupereka kokonatiyo kungathandize kwambiri kusiyana ndi kupereka ndalama. Apatu m’baleyu anaganiza mwanzeru. Nawonso abale a ku Greece amapereka mafuta a maolivi, tchizi komanso zakudya zina ku banja la Beteli. w17.07 8 ¶7-8

Loweruka, November 23

Tiimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni.​—Sal. 137:3.

Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo sankafuna kuimba ngakhale pang’ono. Mitima yawo inali itasweka ndipo chimene ankafuna ndi kulimbikitsidwa basi. Mogwirizana ndi ulosi wa m’Mawu a Mulungu, Mfumu ya ku Perisiya dzina lake Koresi inawapulumutsa. Koresi anagonjetsa Babulo n’kulengeza kuti: “Yehova . . . wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu. . . . Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Yehova Mulungu wake akhale naye. Choncho apite.” (2 Mbiri 36:23) Aisiraeli amene anali ku Babulo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva mawu amenewa. Sikuti Yehova ankangolimbikitsa Aisiraeli monga gulu koma ankalimbikitsanso aliyense payekha. Ndi mmene amachitiranso masiku ano. Mulungu “amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Sal. 147:3) Izi zikusonyeza kuti Yehova amasamalira anthu amene akudwala komanso amene ali ndi nkhawa. Iye amafunitsitsa kutitonthoza komanso kutilimbikitsa tikakhala ndi nkhawa. (Sal. 34:18; Yes. 57:15) Iye amatipatsa nzeru komanso mphamvu kuti tithe kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo.​—Yak. 1:5. w17.07 18 ¶4-5

Lamlungu, November 24

Pakuti kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.​—Luka 12:34.

Yehova ndi wachuma kwambiri kuposa wina aliyense. (1 Mbiri 29:11, 12) Koma popeza ali ndi mtima wopatsa, amagawira anthu ake mowolowa manja chuma chauzimu. Timayamikira kwambiri kuti Yehova watipatsa (1) Ufumu wa Mulungu, (2) utumiki umene umapulumutsa anthu komanso (3) mfundo zamtengo wapatali zomwe zimapezeka m’Mawu ake. Koma kupanda kusamala, tikhoza kusiya kuyamikira chuma chamtengo wapatalichi ndipo zingakhale ngati tachitaya. Choncho tiyenera kuteteza zinthu zamtengo wapatalizi pozigwiritsa ntchito bwino komanso kupitiriza kuzikonda kwambiri. Ambirife tasinthanso zinthu zambiri pa moyo wathu kuti tikhale nzika za Ufumu wa Mulungu. (Aroma 12:2) Komatu ntchito idakalipo. Tiyenera kukhala tcheru nthawi zonse kuti mtima wathu usayambe kukonda zinthu zina monga chuma kapena chiwerewere.​—Miy. 4:23; Mat. 5:27-29. w17.06 9 ¶1; 10 ¶7

Lolemba, November 25

Kodi ukudziwa?​—Yobu 38:21.

Palibe paliponse pamene Mulungu anamufotokozera Yobu chimene chinachititsa kuti avutike choncho. Cholinga chake pomuyankha sichinali kumufotokozera chifukwa chake anakumana ndi mavutowo ngati kuti Mulungu ankafunika kuyankha mlandu kwa Yobu. Koma ankafuna kumuthandiza kuzindikira kuti Yehovayo ndi wamkulu kwambiri poyerekezera ndi Yobuyo. Yehova anathandizanso Yobu kuzindikira kuti panali nkhani zina zimene zinali zofunika kwambiri kuposa mavuto akewo. (Yobu 38:18-20) Mawu a Yehovawa anathandiza Yobu kuti ayambe kuona zinthu moyenera. Popeza Yobu anali atavutika kwambiri, kodi zimene Yehova ananenazo zinali zankhanza komanso zopanda chifundo? Ayi, ndipo nayenso Yobu sanaganize choncho. Ngakhale kuti anali atakumana ndi mavutowo, Yobu anayamikira zimene Yehova anamuuza. Iye anafika ponena kuti: “Ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Izi zikusonyeza kuti malangizo olimbikitsa koma osapita m’mbali a Mulungu anamuthandiza. (Yobu 42:1-6) Yobu anali atalandiranso malangizo ochokera kwa Elihu yemwe anali wamng’ono kwa iye. (Yobu 32:5-10) Yobu atalandira malangizo a Mulungu n’kusintha maganizo ake, Mulunguyo analankhula kwa anthu ena mawu osonyeza kuti akusangalala ndi Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake.​—Yobu 42:7, 8. w17.06 24-25 ¶11-12

Lachiwiri, November 26

Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.​—Luka 10:42.

Kuti tidziwe ngati tili ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimasangalala kwambiri ndikamagwira ntchito, kapena ndimasangalala ndikamachita zinthu zokhudza kulambira?’ Kuganizira kwambiri nkhaniyi kungatithandize kuzindikira zimene timakonda kwambiri. Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Pa nthawi ina, iye anapita kunyumba ya Mariya ndi Marita. Marita anatanganidwa kwambiri ndi kukonza chakudya pomwe Mariya anakhala pansi n’kumamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa. Marita atadandaula kuti Mariya sankamuthandiza, Yesu anamuuza mawu amulemba lalero. (Luka 10:38-42) Apatu Yesu anaphunzitsa Marita mfundo yofunika. Nafenso tiyenera kusankha “chinthu chabwino,” chomwe ndi kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba. Tikatero tidzapewa kusokonezedwa ndi ntchito komanso tidzasonyeza kuti timakonda kwambiri Khristu. w17.05 24 ¶9-10

Lachitatu, November 27

Tamvera malangizo a bambo ako.​—Miy. 1:8.

Yehova wapatsa makolo, osati agogo kapena anthu ena, udindo wophunzitsa ana awo Mawu ake. (Miy. 31:10, 27, 28) Komabe makolo amene sadziwa chilankhulo cha dziko limene asamukiralo mwina angafune kuti anthu ena aziwathandiza kuphunzitsa ana awo mogwira mtima. Izi sizikutanthauza kuti makolo azingosiyira anthu ena udindo wophunzitsa ana awo. Anthu enawo ndi ongothandiza makolowo pa udindo umene ali nawo ‘wolera ana awo m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.’ (Aef. 6:4) Mwachitsanzo, makolo angapemphe akulu mumpingo kuti awapatse malangizo okhudza mmene angachitire kulambira kwa pabanja komanso kuti athandize ana awo kupeza anzawo abwino. Nthawi zina makolo angachitenso bwino kuitana mabanja ena kuti achite nawo kulambira kwa pabanja. Achinyamata angathandizidwenso ndi abale ndi alongo achitsanzo chabwino akamayenda nawo mu utumiki kapena kuchitira nawo limodzi zosangalatsa.​—Miy. 27:17. w17.05 11-12 ¶17-18

Lachinayi, November 28

Uthawire ku Iguputo.—Mat. 2:13.

Mngelo wa Yehova atachenjeza Yosefe kuti Mfumu Herode inkafuna kupha Yesu, Yosefe anathawa ndi banja lake n’kupita ku Iguputo. Iwo anakhalabe komweko mpaka pamene Herode anamwalira. (Mat. 2:14, 19-21) Pa nthawi ina, Akhristu oyambirira “anabalalikira m’zigawo za Yudeya ndi Samariya” chifukwa choti ankazunzidwa. (Mac. 8:1) Yesu anasonyezanso kuti otsatira ake ambiri adzathawa kwawo. Iye anati: “Akakuzunzani mumzinda wina, muthawire mumzinda wina.” (Mat. 10:23) Izi zachitikiranso a Mboni za Yehova ambiri. Ambiri mwa iwo achibale awo anaphedwa ndipo katundu wawo anawonongedwa kapena kulandidwa. Anthu ena anakumana ndi zinthu zoopsa pothawa kwawo komanso atafika kumalo amene anathawirako. Mwachitsanzo, m’makampu, anthu amakonda kumwa mowa, kutchova juga, kuba komanso kuchita zachiwerewere. Koma a Mboniwa sankataya mtima chifukwa ankadziwa kuti tsiku lina adzachoka m’makampuwa ngati mmene zinalili ndi Aisiraeli m’chipululu.​—2 Akor. 4:18. w17.05 3-4 ¶2-5

Lachisanu, November 29

Okonda chilamulo chanu amapeza mtendere wochuluka, Ndipo palibe chowakhumudwitsa.​—Sal. 119:165.

Nthawi zina, ife kapena anthu ena akhoza kuchitiridwa zinthu zimene zingaoneke ngati zopanda chilungamo mumpingo. Zimenezi zikachitika, tisamalole kuti zitifooketse. M’malomwake tiziyesetsa kukhalabe okhulupirika komanso tizidalira Yehova ndipo tizipemphera kwa iye. Tizikumbukiranso kuti sitingadziwe zonse zokhudza nkhaniyo ndipo n’kutheka kuti ifeyo tikungolakwitsa kuganiza kuti pachitika zinthu zopanda chilungamo. Si bwinonso kulankhula zoipa chifukwa zimenezo zingangochititsa kuti zinthu ziipireipire. Komanso m’malo moyamba kupeza njira zathu zothetsera vutolo, tizikhala okhulupirika n’kumayembekezera Yehova moleza mtima. Tikatero tidzasangalatsa Yehova ndipo adzatidalitsa. Tiyeni tonse tizikhulupirira kuti Yehova, yemwe ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” nthawi zonse amachita chilungamo popeza “njira zake zonse ndi zolungama.”​—Gen. 18:25; Deut. 32:4. w17.04 22 ¶17

Loweruka, November 30

Munthu woipa asiye njira yake . . . Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.​—Yes. 55:7.

Kodi anthu amene akukana kusintha zidzawathera bwanji pa nthawi ya chisautso chachikulu? Yehova analonjeza kuti adzawononga dziko loipali. (Sal. 37:10) Mwina anthu ena oipa amaganiza kuti iwowo sadzawonongedwa. N’kutheka kuti ali ndi maganizo amenewa chifukwa choti akhala akuchita zoipa koma salangidwa chifukwa amabisala. Mwinanso n’chifukwa choti sakumana ndi zotsatira za zochita zawozo. (Yobu 21:7, 9) Koma paja Baibulo limati: “Maso ake [a Yehova] amayang’anitsitsa njira za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse. Kulibe mdima wandiweyani woti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.” (Yobu 34:21, 22) Choncho palibe amene adzabisale moti Yehova n’kulephera kumuona. Komanso popeza maso ake amaona paliponse, palibe chimene munthu angachite moti n’kumupusitsa. Choncho Aramagedo ikadzatha, tidzayang’ana paliponse pamene pankakhala anthu oipa, koma sadzapezekapo chifukwa adzakhala atawonongedwa.​—Sal. 37:12-15. w17.04 10 ¶5

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena