Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 98-108
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Lachiwiri, October 1
  • Lachitatu, October 2
  • Lachinayi, October 3
  • Lachisanu, October 4
  • Loweruka, October 5
  • Lamlungu, October 6
  • Lolemba, October 7
  • Lachiwiri, October 8
  • Lachitatu, October 9
  • Lachinayi, October 10
  • Lachisanu, October 11
  • Loweruka, October 12
  • Lamlungu, October 13
  • Lolemba, October 14
  • Lachiwiri, October 15
  • Lachitatu, October 16
  • Lachinayi, October 17
  • Lachisanu, October 18
  • Loweruka, October 19
  • Lamlungu, October 20
  • Lolemba, October 21
  • Lachiwiri, October 22
  • Lachitatu, October 23
  • Lachinayi, October 24
  • Lachisanu, October 25
  • Loweruka, October 26
  • Lamlungu, October 27
  • Lolemba, October 28
  • Lachiwiri, October 29
  • Lachitatu, October 30
  • Lachinayi, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 98-108

October

Lachiwiri, October 1

Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu . . . popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.​—Yak. 1:5.

Yehova ndi wanzeru zopanda malire ndipo amapatsa ena nzeru. Chinthu china chimene chimatithandiza kukhala anzeru ndi malangizo amene Yehova amatipatsa. (Miy. 2:10-12) Munthu akakhala ndi nzeru zimenezi amatetezeka ku zinthu zimene zingawononge makhalidwe ake abwino komanso moyo wake wauzimu. Ndipo chitetezo chimenechi n’chimene chimathandiza kuti Mulungu apitirize kutikonda. (Yuda 21) Ngakhale zili choncho, zinthu monga uchimo umene tinabadwa nawo, kumene tinakulira komanso mavuto ena, zimachititsa kuti tizivutika kulandira malangizo kapena kuona malangizowo m’njira yoyenera. Koma tikazindikira kuti Yehova amatipatsa malangizo chifukwa chotikonda timayamikira kwambiri malangizowo. Paja lemba la Miyambo 3:11, 12 limanena kuti: “Mwana wanga, usakane malangizo a Yehova . . . chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda.” Tisamaiwale kuti Yehova amatikonda ndipo amatifunira zabwino zokhazokha. (Aheb. 12:5-11) Popeza Yehova amatidziwa bwino, amatipatsa malangizo kapena chilango m’njira yoyenera ndipo sapitirira malire. w18.03 28-29 ¶1-2

Lachitatu, October 2

Muzicherezana.​—1 Pet. 4:9.

Mtumwi Petulo analemba mawu apamwambawa ku mipingo ya ku Asia Minor yokhala ndi anthu a mitundu yosiyanasiyana. Anthuwa ankakumana ndi mayesero oopsa ngati “moto.” Kodi n’chiyani chimene chikanathandiza Akhristu onse kuti apirire mavutowa? (1 Pet. 1:1; 4:4, 7, 12) Petulo anauza Akhristu anzake kuti ‘azichereza’ anthu amene ankadziwana nawo. Ndiye kodi kucherezana kukanawathandiza bwanji? Kukanawathandiza kuti azigwirizana kwambiri. Taganizirani zimene zinakuchitikirani inuyo. Kodi munaitanidwapo kuti mukacheze kunyumba ya munthu wina? Muyenera kuti mukukumbukirabe mmene munasangalalira. Kapena mwina munaitana anthu ena amumpingo kuti adzacheze nanu ndipo zinathandiza kuti muzigwirizana kwambiri. Tikaitanira abale ndi alongo athu kunyumba m’pamene timadziwana nawo bwino kwambiri. Akhristu a mu nthawi ya Petulo ankafunika kugwirizana kwambiri kuti athe kupirira mavuto awo. Ifenso timafunika kugwirizana kwambiri chifukwa tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’​—2 Tim. 3:1. w18.03 14-15 ¶1-3

Lachinayi, October 3

Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.​—Mat. 5:3.

Baibulo limasonyeza ubwino wokhala munthu wauzimu. Mwachitsanzo, lemba la Aroma 8:6 limanena kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.” Munthu akamaika maganizo pa zinthu zauzimu amakhala pa mtendere ndi Mulungu, amakhala ndi mtendere mumtima komanso amakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Koma dziko limene tikukhalamoli ndi loipa kwambiri. Popeza anthu osaopa Mulungu ali ponseponse, tiyenera kuchita khama kwambiri kuti tikhale auzimu komanso kuti tisabwerere m’mbuyo. Munthu akasiya kuganizira kwambiri za Mulungu amapereka mpata m’maganizo mwake kuti mpweya woipa wa m’dzikoli ulowemo. Yuda anafotokoza za anthu ena amene amayamba kukonda kwambiri za m’dzikoli moti sakhalanso ndi mzimu wa Mulungu.​—Yuda 18, 19. w18.02 19 ¶5; 20 ¶7-8

Lachisanu, October 4

Anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.​—2 Tim. 3:13.

Anthu ambiri ogwira ntchito kuchipatala amasamalira anthu amene akudwala matenda opatsirana. Iwo amasamalira anthuwo chifukwa chofuna kuwathandiza. Koma pochita zimenezi, amayenera kudziteteza kuti asatengere matenda amene anthuwo akudwala. Chimodzimodzinso ndi ifeyo. Timakhala komanso kugwira ntchito ndi anthu amene ali ndi maganizo ndiponso makhalidwe oipa. Choncho tiyenera kukhala osamala kwambiri. M’masiku otsiriza ano makhalidwe a anthu aipa kwambiri. M’kalata yake yachiwiri yopita kwa Timoteyo, Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu omwe satumikira Mulungu adzakhale nawo m’masiku otsiriza, ndipo anati makhalidwewa adzaipa kwambiri. (2 Tim. 3:1-5, 13) Mwina Akhristufe timakhumudwa ndi makhalidwe oipa amene anthu ambiri ali nawo. Komabe tikhoza kutengera mosavuta maganizo ndiponso zochita za anthu omwe ali ndi makhalidwewo. (Miy. 13:20) Choncho tiyenera kudziteteza kuti tisamatengere makhalidwe oipawo komanso tiyenera kuthandiza anthu ena kuti akhale ndi makhalidwe abwino. w18.01 27 ¶1-2

Loweruka, October 5

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.​—Mat. 28:19.

Mu 33 C.E., Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa anthu oposa 500, omwe anali amuna, akazi ndipo mwinanso ana. N’kutheka kuti pa nthawiyi m’pamene ananena mawu ali pamwambawa. (1 Akor. 15:6) Choncho zikuoneka kuti otsatira a Yesu ambirimbiri analipo pamene Yesu anapereka lamulo loti aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake. Yesu anasonyeza kuti munthu amene akufuna kukhala Mkhristu ayenera kubatizidwa. (Mat. 11:29, 30) Munthu aliyense amene ankafuna kutumikira Mulungu movomerezeka ankayenera kuzindikira udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Yehova. Munthu sankabatizidwa popanda kuchita zimenezi ndipo umenewu ndi ubatizo wokhawo umene Yehova ankauvomereza. Baibulo limapereka umboni wakuti munthawi ya atumwi ophunzira atsopano a Khristu ankamvetsa tanthauzo la kubatizidwa ndipo sankazengereza kubatizidwa.​—Mac. 2:41; 9:18; 16:14, 15, 32, 33. w18.03 5 ¶8

Lamlungu, October 6

Iwe Danieli, munthu wokondedwa kwambiri.​—Dan. 10:11.

Masiku ano tikukhala m’dziko limene laipitsidwa kwambiri ndi Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga ndipo amatchedwa “malo okhala ziwanda.” (Chiv. 18:2) Choncho nafenso timakhala osiyana kwambiri ndi anthu ena ndipo nthawi zina timanyozedwa. (Maliko 13:13) Mofanana ndi Danieli, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu wathu. Tikamadalira Yehova modzichepetsa ndiponso kumumvera, nafenso timakhala amtengo wapatali kwa iye. (Hag. 2:7) Makolo angaphunzire zambiri pa chitsanzo cha makolo a Danieli. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngakhale kuti ku Yuda zinthu zinali zoipa kwambiri pamene Danieli anali wamng’ono, iye anaphunzira kukonda Mulungu. Zimenezi sizinangochitika pa zokha ayi. Koma makolo ake ayenera kuti ankamuphunzitsa bwino. (Miy. 22:6) Ngakhale dzina la Danieli lomwe limatanthauza kuti “Mulungu Ndi Woweruza Wanga” limasonyeza kuti makolo ake ankakonda Mulungu. Choncho ngati ndinu makolo, musataye mtima koma pitirizani kuphunzitsa ana anu moleza mtima. (Aef. 6:4) Muyeneranso kumapemphera nawo komanso kuwapempherera. Mukamayesetsa kuwafika pamtima ndi mfundo za m’Baibulo Yehova adzakudalitsani.​—Sal. 37:5. w18.02 5 ¶12; 6 ¶14-15

Lolemba, October 7

Chilichonse n’chochokera kwa inu, ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu.​—1 Mbiri 29:14.

Kupereka zinthu kwa Yehova ndi mbali ya kulambira kwathu. M’masomphenya, mtumwi Yohane anamva atumiki a Yehova kumwamba akunena kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chiv. 4:11) Tikamapatsa Yehova zinthu zabwino kwambiri, timakhala tikumupatsa ulemerero ndi ulemu womuyenerera. Yehova anauza Mose kuti alamule Aisiraeli kuti azikaonekera kwa Yehova pa zikondwerero zitatu zimene zinkachitika chaka chilichonse. Aisiraeliwo sankayenera kupita kukalambira Yehova “chimanjamanja.” (Deut. 16:16) Masiku anonso, kupereka zinthu mowolowa manja pothandiza pa ntchito ya gulu la Yehova ndi mbali yofunika ya kulambira kwathu. w18.01 18 ¶4-5

Lachiwiri, October 8

Ndidzakutsitsimutsani.​—Mat. 11:28.

Yesu ananenanso kuti: “Senzani goli langa. . . . pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:29, 30) Mfundo imeneyi ndi yoona. Nthawi zina timakhala otopa kwambiri tikamanyamuka kupita kumisonkhano kapena mu utumiki. Koma kodi timamva bwanji tikamabwerera kunyumba? Timamva bwino ndipo zimatithandiza kupirira mavuto athu. Izi zikusonyeza kuti goli la Yesu ndi lofewadi. Mlongo wina, yemwe tangomupatsa dzina loti Kayla, amadwala matenda enaake ofooketsa thupi, amavutika maganizo komanso mutu waching’alang’ala umamupweteka pafupipafupi. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zina amavutika kuti apezeke pamisonkhano. Koma atayesetsa tsiku lina kuti akapezeke kumisonkhano, analemba kuti: “Nkhani imene inakambidwa inali yolimbikitsa anthu amene ayamba kutaya mtima. Wokambayo anafotokoza zinthu mosonyeza kuti amamvera chisoni kwambiri anthu oterewa moti ndinayamba kulira. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti kupezeka pamisonkhano ndi kothandiza kwambiri.” Kayla anasangalala kuti anayesetsa kufika kumisonkhanoyo. w18.01 8-9 ¶6-7

Lachitatu, October 9

Phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka.​—Sal. 73:2.

Kodi mungatani ngati mwana wanu wobatizidwa wayamba kukayikira zimene amakhulupirira? Mwachitsanzo, wachinyamata wobatizidwa akhoza kuyamba kukopeka ndi zinthu za m’dzikoli kapena kukayikira zoti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza. (Sal. 73:1-3, 12, 13) Zimenezi zikachitika, yankho limene makolo angapereke lingachititse kuti mwanayo ayambe kukhulupirira kwambiri mfundo za m’Malemba kapena asiye kuzikhulupirira. Koma kaya mwanayo ndi wamng’ono kapena wamkulu, simuyenera kukangana naye pa nkhani imeneyi. Cholinga chanu chizikhala kumuthandiza mwachikondi kuti asinthe maganizo akewo. N’zoona kuti mwana amene wabatizidwa amakhala atadzipereka kwa Yehova. Ndipo podziperekapo amalonjeza kuti azikonda Mulungu komanso kuika patsogolo zofuna zake. (Maliko 12:30) Yehova amaona kuti lonjezo limeneli ndi lofunika kwambiri ndipo ndi mmene aliyense ayenera kulionera.–Mlal. 5:4, 5. w17.12 22 ¶16-17

Lachinayi, October 10

Ndikudziwa kuti [mchimwene wanga] adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.​—Yoh. 11:24.

Mofanana ndi Marita, atumiki a Yehova okhulupirika ankadziwa kuti idzafika nthawi pamene akufa adzauka. Taganizirani zimene Mulungu anauza Abulahamu kuti achite. Paja anamuuza kuti: “Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo, ndipo . . . ukamupereke nsembe yopsereza.” (Gen. 22:2) Popeza Isaki anali mwana amene Abulahamu ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali, kodi mukuganiza kuti iye anamva bwanji Mulungu atamuuza zimenezi? Yehova anali atalonjeza Abulahamu kuti mbewu yake idzathandiza kuti anthu a mitundu yonse adalitsidwe. (Gen. 13:14-16; 18:18; Aroma 4:17, 18) Ananenanso kuti mbewuyo “idzachokera mwa Isaki.” (Gen. 21:12) Ndiye kodi zonsezi zikanatheka bwanji ngati Abulahamu akanapha Isaki? Paulo ananena kuti Abulahamu ankakhulupirira kuti Mulungu akhoza kuukitsa Isaki. (Aheb. 11:17-19) Abulahamu sankadziwa kuti mwana wakeyo adzaukitsidwa liti koma sankakayikira kuti Yehova adzamuukitsa. w17.12 5-6 ¶12-14

Lachisanu, October 11

Ine ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse.—Mac. 20:26.

Mofanana ndi Paulo, tiyenera kuyesetsa kuti tiziona moyo mmene Mulungu amauonera. Yehova “amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Kodi inunso mumafuna zimenezi? Mukamayesetsa kukhala ndi mtima wachifundo mudzafunitsitsa kulalikira mwakhama komanso mudzasangalala kwambiri pochita zimenezi. Timasonyezanso kuti timaona moyo mmene Mulungu amauonera tikamayesetsa kupewa ngozi. Tiyenera kuchita zinthu mosamala tikakhala pa ulendo kapena tikamagwira ntchito. Tizichita zimenezi ngakhale pamene tikupita kumalo olambirira, kumanga malowo kapena kuwakonza. Sitiyenera kuika moyo wathu pa ngozi pongofuna kuti ntchito iyende kapena tisawononge ndalama. Tiyenera kuyesetsa kutsanzira Mulungu wathu wolungama amene nthawi zonse amachita zinthu zoyenera m’njira yoyenera. Ndipo akulu ayenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopewa kuika pa ngozi moyo wawo kapena wa anthu ena. (Miy. 22:3) Choncho ngati mkulu wakukumbutsani malangizo othandiza kupewa ngozi, muyenera kumvera. (Agal. 6:1) Kuona moyo mmene Yehova amauonera kudzakuthandizani kuti “musakhale ndi mlandu wamagazi.”​—Deut. 19:10. w17.11 16 ¶11-12

Loweruka, October 12

Musalole kuti munthu aliyense akumanitsenimphoto.—Akol. 2:18.

Mofanana ndi mtumwi Paulo, odzozedwa akuyembekezera kulandira “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba.” (Afil. 3:14) Iwo akuyembekezera kukalamulira limodzi ndi Yesu Khristu kumwamba komanso kudzagwira nawo ntchito yothandiza anthu kuti akhalenso angwiro. (Chiv. 20:6) Kunena zoona, Yehova wawapatsa chiyembekezo chabwino kwambiri. Koma nawonso a nkhosa zina akuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri. Iwo akuyembekezera mphoto ya moyo wosatha padziko lapansi. (2 Pet. 3:13) Pofuna kuthandiza odzozedwa anzake kuti akhalebe okhulupirika n’kukalandira mphoto yawo, Paulo anawauza kuti: “Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba.” (Akol. 3:2) Iwo anafunika kuganizira nthawi zonse zinthu zamtengo wapatali zimene akuyembekezera kumwamba. (Akol. 1:4, 5) Kuganizira kwambiri madalitso amene Yehova watilonjeza kungatithandize kuti chilichonse chisatilepheretse kudzalandira mphotoyo.​—1 Akor. 9:24. w17.11 25 ¶1-2

Lamlungu, October 13

Imbirani Yehova.​—Sal. 96:1.

Nyimbo zambiri za m’buku latsopano lakuti Imbirani Yehova Mosangalala zinalembedwa kuti zikhale ngati mapemphero. Nyimbo zimenezi zikuthandizani kuti muziuza Yehova zimene zili mumtima mwanu. Nyimbo zina ‘zimatilimbikitsa pa chikondi ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Tiyenera kuyesetsa kuzidziwa bwino ndipo tikhoza kuchita zimenezi pomvetsera nyimbozi pa jw.org. Tikamayeserera nyimbozi kunyumba, tingathe kumaimba ndi mtima wonse popanda kudzikayikira. Tisaiwale kuti kuimba ndi kofunika kwambiri polambira Yehova. Zili choncho chifukwa ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti timamukonda ndiponso kumuyamikira. (Yes. 12:5) Mukamaimba mosangalala, mudzalimbikitsa anthu ena kuti nawonso aziimba ndi mtima wonse. Aliyense mumpingo, kaya achinyamata, achikulire komanso atsopano akhoza kulambira Yehova pomuimbira nyimbo. Choncho tiyeni tisamachite manyazi poimbira Yehova mosangalala. w17.11 7 ¶18-19

Lolemba, October 14

Khalani ochenjera ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.—Mat. 10:16.

Anthu ambiri amene amathawa kwawo amachokera m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Koma chosangalatsa n’chakuti abale ndi alongo a m’mayiko amene amathawirawo amachita khama powathandiza kuti ayambe kumva “mawu a Ufumu.” (Mat. 13:19, 23) Anthu ambiri “olemedwa” amatsitsimulidwa pamisonkhano ndipo sachedwa kuvomereza kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (Mat. 11:28-30; 1 Akor. 14:25) Koma tikamalalikira kwa anthu othawa kwawo tiyenera kukhala “ochenjera” komanso osamala. (Miy. 22:3) Tiyenera kuwamvetsera moleza mtima koma si bwino kukambirana nawo za ndale. Ndi bwino kutsatira malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi komanso kwa akuluakulu a boma ndipo tizipewa kuika moyo wathu kapena wa anthu ena pa ngozi. Tiziyesetsa kulemekeza zimene anthuwo amakhulupirira komanso chikhalidwe chawo. Mwachitsanzo, anthu ochokera m’mayiko ena amakhala ndi maganizo amphamvu pa nkhani ya zovala za akazi. Choncho polalikira kwa anthu oterowo ndi bwino kuvala zovala zimene sizingawakhumudwitse. w17.05 7 ¶17-18

Lachiwiri, October 15

Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo.​—Akol. 4:6.

Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera n’cholinga choti tikamalankhula ndi achibale athu omwe si Mboni, tizisonyeza makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. Si bwino kutsutsana nawo pa mfundo zilizonse zabodza zimene amakhulupirira. Iwo akalankhula kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa tiyenera kutsanzira atumwi. Paja Paulo analemba kuti: “Pamene akutinenera zachipongwe, timadalitsa. Pozunzidwa, timapirira. Ponyozedwa, timayankha mofatsa.” (1 Akor. 4:12, 13) N’zoona kuti kulankhula mofatsa kumathandiza pochita zinthu ndi achibale amene si Mboni. Koma kukhala ndi khalidwe labwino ndi kumene kumathandiza kwambiri. (1 Pet. 3:1, 2, 16) Tiziyesetsa kuchita zimene tingathe kuti achibale athu aone kuti a Mboni za Yehova amakhala ndi mabanja osangalala, amasamalira ana awo, amakhala ndi makhalidwe abwino komanso amakhala osangalala. Ngakhale achibale athu atapanda kuphunzira Baibulo tikhoza kukhala osangalala podziwa kuti tasangalatsa Yehova chifukwa cha kukhulupirika kwathu. w17.10 15 ¶13-14

Lachitatu, October 16

Usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu.​—2 Tim. 2:15.

Kodi tiyenera kudabwa tikaona anthu akusintha kwambiri chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu? Ayi. Paja ngakhale mu nthawi ya atumwi, abale ndi alongo omwe anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba, anali atasinthanso. (1 Akor. 6:9-11) Mtumwi Paulo atatchula anthu osiyanasiyana amene sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu ananena kuti: “Ena mwa inu munali otero.” Iwo anasintha chifukwa chothandizidwa ndi Malemba komanso mzimu woyera wa Mulungu. Ena analinso ndi mavuto aakulu ngakhale pambuyo polowa mumpingo wachikhristu. Mwachitsanzo, Baibulo limatchula za Mkhristu wina amene anachotsedwa koma patapita nthawi anabwezeretsedwa. (1 Akor. 5:1-5; 2 Akor. 2:5-8) Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira mavuto amene Akhristu anzathu anali nawo n’kuona mmene Mawu a Mulungu anawathandizira kuti asinthe. Nafenso tiyenera kugwiritsa ntchito bwino Mawuwo. w17.09 23-24 ¶2-3

Lachinayi, October 17

Tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18.

Chikondi chimene munthu amachisonyeza chifukwa chotsatira mfundo zabwino (a·gaʹpe) ndi mphatso yochokera kwa Yehova. Paja Yehova ndi amene anayambitsa chikondi chimenechi. (1 Yoh. 4:7) Chikondichi ndi chapamwamba kwambiri. Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi amachitira ena zabwino popanda kufuna phindu lililonse, ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anthu amene si anzake. Buku lina limanena kuti “zochita za munthu n’zimene zimasonyeza” kuti ali ndi chikondi cha a·gaʹpe. Tikamasonyeza chikondi chimenechi kapena munthu wina akatisonyeza chikondichi timakhala osangalala. Yehova asanalenge Adamu ndi Hava anali atasonyeza kale kuti amakonda anthu. Iye analenga dziko n’cholinga choti anthu akhalemo mpaka kalekale komanso mosangalala. Yehova anachita zimenezi kuti atithandize ifeyo, osati kuti apindulepo kenakake. Iye anasonyezanso chikondi chapamwamba popereka mwayi kwa anthu woti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso amene anawakonzera. w17.10 7 ¶1-2

Lachisanu, October 18

Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.​—Yak. 2:8.

Yakobo ananenanso kuti: “Mukapitiriza kukhala okondera, mukuchita tchimo.” (Yak. 2:8, 9) Chikondi chimatithandiza kuti tisamakondere anthu chifukwa cha maphunziro awo, mtundu wawo kapena chuma chawo. Koma munthu ayenera kukhala wopanda tsankho kuchokera mumtima osati kungodzionetsera kuti alibe tsankho. Baibulo limanenanso kuti ‘chikondi n’choleza mtima, n’chokoma mtima komanso sichidzikuza.’ (1 Akor. 13:4) N’zosatheka kupitiriza kulalikira uthenga wa Ufumu ngati munthu si woleza mtima, wokoma mtima komanso wodzichepetsa. (Mat. 28:19) Makhalidwe amenewa amathandizanso kuti tizikhala bwinobwino ndi abale ndi alongo onse mumpingo. Kodi chimachitika n’chiyani tikamasonyeza chikondi m’njira imeneyi? Mipingo imakhala yogwirizana kwambiri ndipo izi zimalemekeza Yehova komanso kuthandiza kuti anthu ena ayambe kumutumikira. M’pomveka kuti Baibulo likamafotokoza za umunthu watsopano limamaliza ndi mfundo yamphamvu yakuti: “Kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”​—Akol. 3:14. w17.08 26 ¶18-19

Loweruka, October 19

Yehova [anawatumizira] machenjezo . . . mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo.​—2 Mbiri 36:15.

Nafenso tiyenera kuchitira chifundo anthu amene akhoza kulapa machimo awo n’kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Yehova safuna kuti aliyense adzawonongedwe pa chisautso chachikulu. (2 Pet. 3:9) Choncho panopa tiyeni tipitirize kuchitira anthu chifundo polalikira uthenga wochenjeza. Yesu anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani ya chifundo. Iye anamvera chisoni anthu ambiri amene anakumana nawo chifukwa “anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” Ndiye kodi iye anatani? Baibulo limanena kuti: “Anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Mat. 9:36; Maliko 6:34) Yesu anali wosiyana kwambiri ndi Afarisi omwe sankafuna ngakhale pang’ono kuthandiza anthu wamba. (Mat. 12:9-14; 23:4; Yoh. 7:49) Kodi inuyo mumachitiranso chifundo anthu amene ali ndi njala yofuna kumva Mawu a Yehova? w17.09 9 ¶6; 10 ¶9

Lamlungu, October 20

Ndikayamba kuchitapo kanthu, ndani amene angalimbane ndi dzanja langa?​—Yes. 43:13.

Yosefe ali m’ndende ku Iguputo, Yosefe ayenera kuti sankaganiza n’komwe zoti adzakhala wachiwiri kwa mfumu ya Iguputo komanso kuti Yehova adzamugwiritsa ntchito kuti apulumutse achibale ake kuti asafe ndi njala. (Gen. 40:15; 41:39-43; 50:20) N’zosachita kufunsa kuti zimene Yehova anamuchitira zinali zosiyana kwambiri ndi zimene Yosefe ankayembekezera. Taganiziranso za Sara yemwe anali agogo a Yosefe. Kodi mukuganiza kuti iye ankayembekezera kuti Yehova angachititse kuti abereke mwana? Mosakayikira kubadwa kwa Isaki kunaposa chilichonse chimene Sara ankaganizira. (Gen. 21:1-3, 6, 7) N’zoona kuti sitingayembekezere kuti Yehova adzathetsa mavuto athu onse dziko latsopano lisanafike ndipo sitipempha kuti atichitire zinthu zodabwitsa. Koma timadziwa kuti Mulungu wathuyu ndi amenenso anathandiza atumiki ake modabwitsa m’mbuyomo. (Yes. 43:10-13) Kudziwa mfundo imeneyi kumatithandiza kuti tizimukhulupirira kwambiri. Timadziwanso kuti iye akhoza kuchita chilichonse chimene chingafunike potithandiza kuti tizichita zimene amafuna. (2 Akor. 4:7-9) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani za m’Baibulo zimene takambiranazi? Nkhani ya Hezekiya, Yosefe ndi Sara zikusonyeza kuti tikakhala okhulupirika kwa Yehova, iye angatithandize kuchita zinthu zimene zingaoneke kuti n’zosatheka. w17.08 11-12 ¶13-14

Lolemba, October 21

Pereka ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.​—Miy. 16:3.

Mukamachita utumiki, mumagwira ntchito ndi atumiki a nthawi zonse ena ndipo izi zimakuthandizani kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu. Ambiri azindikira kuti kutumikira Yehova mwakhama ali achinyamata kwawathandiza kukhala ndi mabanja abwino. Ndipo anthu ambiri amene amachita upainiya asanalowe m’banja amadzapitiriza utumikiwu limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wawo. (Aroma 16:3, 4) Lemba la Salimo 20:4 limanena kuti Yehova “akupatseni zokhumba za mtima wanu, ndipo akwaniritse zofuna zanu.” Zolinga za munthu zimayambira mumtima. Choncho muyenera kuganizira kwambiri zimene mudzachite pa moyo wanu. Muziganizira zimene Yehova akuchita masiku ano komanso mmene mungathandizire pa ntchito yake. Ndiyeno muzikhala ndi zolinga zimene zingamusangalatse. Mukamatumikira Yehova mwakhama mudzamulemekeza kwambiri ndipo mudzakhala wosangalala. Choncho yesetsani kuti mukhale ‘osangalala mwa Yehova, ndipo iye adzakupatsani zokhumba za mtima wanu.’​—Sal. 37:4. w17.07 26 ¶15-18

Lachiwiri, October 22

Tamandani Ya . . . N’kosangalatsa. Kumutamanda n’koyenera.’—Sal. 147:1.

Anthufe timakonda kuyamikira munthu akagwira bwino ntchito inayake, kapena akasonyeza makhalidwe abwino kwambiri. Ngati timachita zimenezi ndi anthu, kuli bwanji Yehova Mulungu? Tiyenera kumutamanda chifukwa ali ndi mphamvu zopanda malire ndipo tikayang’ana zinthu zodabwitsa zimene analenga timaona umboni wa mphamvuzo. Tiyeneranso kumutamanda chifukwa cha chikondi chake ndipo umboni wa chikondicho timauona tikaganizira zoti anapereka Mwana wake kuti akhale dipo lotipulumutsa. Munthu amene analemba Salimo 147 anaona kuti ndi bwino kutamanda Yehova. Iye analimbikitsanso anthu ena kuti azitamanda Mulungu. (Sal. 147:7, 12) Sitikudziwa kuti amene analemba salimoli ndi ndani. Koma zikuoneka kuti munthuyu anali ndi moyo pa nthawi imene Aisiraeli anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo ku Babulo. (Sal. 147:2) Munthu amene analemba salimoli ayenera kuti ankatamanda Yehova chifukwa choyamikira kuti Aisiraeli anabwerera kumalo amene angathe kulambira Mulungu woona. Nanga inuyo muli ndi zifukwa ziti zonenera kuti “Tamandani Ya”?​—Sal. 147:1. w17.07 17 ¶1-3

Lachitatu, October 23

Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama, kuti chumacho chikatha, [Yehova ndi Yesu] akakulandireni m’malo okhala amuyaya.​—Luka 16:9.

Yesu ankadziwa kuti otsatira ake ambiri adzafunika kugwira ntchito m’dziko lopanda chilungamoli kuti azipeza zofunika pa moyo. Ngakhale kuti Yesu sananene chifukwa chake ananena kuti “chuma chosalungama,” Baibulo limasonyeza kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azichita malonda. Yehova anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zonse zimene ankafunikira pa moyo wawo. (Gen. 2:15, 16) Pakati pa Akhristu odzozedwa oyambirira “panalibe ngakhale mmodzi wonena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.” (Mac. 4:32) Mneneri Yesaya analosera za nthawi imene anthu onse sadzasowa chilichonse. (Yes. 25:6-9; 65:21, 22) Koma panopa otsatira a Yesu ayenera kuchita zinthu mwanzeru pogwiritsa ntchito “chuma chosalungama” kuti apeze zofunika pa moyo kwinaku akutumikira Mulungu.​—Luka 16:8. w17.07 8 ¶4-6

Lachinayi, October 24

Chilichonse chimene ali nacho chikhale m’manja mwako.—Yobu 1:12.

M’buku la Yobu, lomwe linalembedwa kalekale, timamva kuti Satana ananena kuti Yobu akhoza kukana ulamuliro wa Mulungu ngati atayesedwa kwambiri. Iye anauza Mulungu kuti azunze Yobu. Koma Yehova sanachite zimenezi. M’malomwake analola kuti Satana ayese Yobu. Pasanapite nthawi yaitali, ziweto zina za Yobu zinabedwa ndipo zina zinaphedwa. Antchito ake komanso ana ake anaphedwanso. Satana anachita zonsezi m’njira yoti zizioneka kuti Mulungu ndi amene wachititsa mavutowo. (Yobu 1:13-19) Kenako Satana anachititsa kuti Yobu adwale matenda onyansa komanso opweteka. (Yobu 2:7) Mavuto ake anawonjezereka pamene mkazi wake komanso anzake atatu anamulankhula mawu opweteka. (Yobu 2:9; 3:11; 16:2) Kodi nkhaniyi inatha bwanji? Zimene Satana ananena zinaonekeratu kuti ndi zabodza. Yobu sanalole kuti asiye kutumikira Yehova.​—Yobu 27:5. w17.06 24 ¶9-10

Lachisanu, October 25

Ngati munthu sasamalira anthu . . . a m’banja lake, wakana chikhulupiriro.—1 Tim. 5:8.

Masiku ano amuna amadziwa kuti Malemba amanena kuti ali ndi udindo wopezera mabanja awo zofunika pa moyo. Iwo ayenera kugwira ntchito mwakhama kuti akwaniritse udindowu. Komabe m’masiku otsiriza ano kuchita zimenezi si kophweka. Popeza ntchito zikusowa, anthu ambiri amalolera kugwira ntchito maola ambiri koma malipiro ake ali ochepa. Komanso mabwana amafuna kuti anthu azichita zambiri pa nthawi yochepa. Izi zimachititsa kuti anthuwo akhale otopa komanso akhale ndi nkhawa. Anthu amene amaona kuti sangakwanitse kuchita zimene abwana awo amafuna akhoza kuchotsedwa ntchito. Koma Akhristufe tiyenera kukhala okhulupirika kwambiri kwa Yehova Mulungu osati kwa mabwana athu. (Luka 10:27) Ntchito imangotithandiza kuti tizipeza zofunika pa moyo n’cholinga choti tizitumikira bwino Mulungu. Koma tikapanda kusamala ntchito yathu ikhoza kutisokoneza potumikira Yehova. w17.05 23 ¶5-7

Loweruka, October 26

Mvera bambo ako amene anakubereka, ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.—Miy. 23:22.

Anthu ena amene angolowa kumene m’gulu la Yehova angapemphe Akhristu ena kuti aziwathandiza kuphunzitsa ana awo Baibulo. Munthu akapemphedwa ndi makolo ena kuti aziphunzira ndi ana awo, sayenera kuchita zinthu ngati watenga udindo wa makolowo. (Aef. 6:1-4) Nthawi zina, Mkhristu angapemphedwe kuti aziphunzira ndi ana amene makolo awo si Mboni. Akhristu oterewa ayenera kukumbukira kuti udindo wawo ndi wophunzitsa Baibulo osati kukhala makolo a anawo. Ndipo ndi nzeru kuphunzira ndi anawo kunyumba kwawo pali makolo awo kapena Mkhristu wina wodalirika, apo ayi angaphunzire nawo pamalo ena oonekera. Zimenezi zingathandize kuti anthu ena asamawakayikire. Komabe zingakhale bwino ngati patapita nthawi, makolo angayambe kukwaniritsa okha udindo wawo wophunzitsa ana. w17.06 8 ¶15-16

Lamlungu, October 27

Ngati sindikudziwa tanthauzo la chinenero, . . . wolankhulayo amakhala mlendo kwa ine.—1 Akor. 14:11.

Ngati ana samvetsa bwino chikhalidwe cha makolo awo mwina sangafune kuphunzira chilankhulo chawo komanso zimene amakhulupirira. Makolo ayenera kuchita zimene zingathandize ana awo kuti azitumikira Yehova osati zongosangalatsa iwowo. (1 Akor. 10:24) M’bale wina dzina lake Samuel anati: “Ine ndi mkazi wanga tinkachita chidwi kuti tidziwe chilankhulo chimene chingathandize ana athu kuti azitumikira bwino Mulungu ndipo tinapemphera kuti Mulungu atipatse nzeru. . . . Titaona kuti ana athu sankamvetsa bwino misonkhano m’chilankhulo chathu, tinasankha zosamukira mumpingo wachilankhulo cha dziko limene tinkakhala. Nthawi zonse tinkapita limodzi ndi ana athu kumisonkhano komanso mu utumiki. Tinkaitananso anthu amumpingowo kuti adzadye nafe kunyumba kwathu komanso kuti apite nafe kwinakwake kukacheza. Zonsezi zinathandiza ana athu kuti adziwane ndi abale ndi alongo. Zinawathandizanso kudziwa bwino Yehova n’kumamuona kuti ndi Mulungu wawo, Atate wawo komanso Mnzawo wapamtima. Tinaona kuti zimenezi n’zofunika kwambiri kuposa kudziwa bwino chilankhulo chathu.” w17.05 10 ¶11-13

Lolemba, October 28

Tamandani Yehova.—Ower. 5:2.

Posachedwapa, padziko lonse padzakhala anthu amene asankha ulamuliro wa Yehova. Timalakalaka kwambiri nthawi imeneyi itafika. Timamva ngati Debora ndi Baraki amene anaimba kuti: “Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe chimodzimodzi, ndipo okukondani inu akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalira.” (Ower. 5:31) Pemphero limeneli lidzayankhidwa Yehova akadzawononga dziko la Satanali. Nkhondo ya Aramagedo ikadzayamba, sipadzafunika anthu oti adzipereke kuti amenye nawo nkhondoyo. M’malomwake, idzakhala nthawi yoti ‘tiime chilili ndi kuona Yehova akutipulumutsa.’ (2 Mbiri 20:17) Choncho nthawi yoti tithandize pokwaniritsa cholinga cha Yehova ndi inoyo ndipo tiyenera kuchita zimenezi mwakhama komanso molimba mtima. Debora ndi Baraki anayamba nyimbo yawo ndi mawu otamanda Yehova osati anthu. Iwo anati: “Chifukwa cha kudzipereka mwaufulu kwa anthu, tamandani Yehova.” (Ower. 5:1, 2) Masiku anonso timafuna kuti anthu akaona mtima wathu wodzipereka, ‘azitamanda Yehova.’ w17.04 32 ¶17-18

Lachiwiri, October 29

Kuno palibe chilichonse chimene ndinalakwa choti andiikire m’ndende muno.​—Gen. 40:15.

N’zoona kuti Yosefe ankakumbukira zoipa zimene anthu anamuchitira pa zaka 13 zimene ankazunzika, koma sanalole kuti zimuchititse kukhala wokwiya. (Gen. 45:5-8) Chofunika kwambiri n’choti sanalole kuti zochita za anthu ena zisokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Patapita nthawi, Yehova anathetsa mavuto a Yosefe komanso anamudalitsa iyeyo ndi banja lake. Zonsezi zinatheka chifukwa choti Yosefe anali wokhulupirika. Ifenso tiziona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndi wofunika kwambiri ndipo tiziuteteza. Tisamalole kuti zochita za ena zitisiyanitse ndi Mulungu wathu amene timamukonda komanso kumulambira. (Aroma 8:38, 39) M’malomwake Akhristu anzathu akatichitira zinthu zopanda chilungamo, tizitsanzira Yosefe. Tizidalira Yehova komanso tiziyesetsa kukhala ndi maganizo ake pa nkhaniyo. Tikachita zonse zimene tingathe mogwirizana ndi Malemba, tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova ndipo tizikhulupirira kuti iye adzakonza zinthu pa nthawi yake komanso m’njira yoyenera. w17.04 20 ¶12; 22 ¶15-16

Lachitatu, October 30

Ngati simudzaiwala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.—1 Sam. 1:11.

Hana anakwaniritsa lonjezo lake kwa Mulungu. Iye sanayambe kupeza zifukwa zoti alephere kuchita zomwe analonjeza. Anatenga Samueli n’kupita naye ku Silo n’kukamupereka kwa Mkulu wa Ansembe dzina lake Eli. Iye anauza Eli kuti: ‘Ndinali kupemphera kuti Yehova andipatse mwana uyu. Ndipo ine ndikum’pereka kwa Yehova. Ndam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.’ (1 Sam. 1:24-28) Kumeneko, “Samueli anapitiriza kukula, akukondedwa ndi Yehova.” (1 Sam. 2:21) Koma kodi zinali zophweka kuti Hana apereke mwana wake? Ayi. Iye ankam’konda kwambiri mwanayu. Koma tsopano sakanathanso kumacheza naye tsiku ndi tsiku. Analibenso mwayi woti azimunyamula, kusewera naye, kumusamalira komanso kuona zinthu zosangalatsa zimene mwana amachita akamakula. Komabe Hana sanayambe kuganiza kuti mwina analakwitsa pa zomwe analonjeza. Mtima wake unkakondwera mwa Yehova podziwa kuti wakwaniritsa lonjezo lake.​—1 Sam. 2:1, 2; Sal. 61:1, 5, 8. w17.04 5 ¶7-8

Lachinayi, October 31

Koma dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.​—2 Tim. 3:1.

Mtumwi Paulo ananeneratu kuti masiku ano adzakhala “nthawi yapadera komanso yovuta.” Iye analembanso kuti “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.” (2 Tim. 3:2-5, 13) Kodi inuyo mwaonapo umboni wa zimenezi? Ambirife tavutikapo chifukwa cha zochita za anthu achiwawa, okwiya komanso achiwembu. Ena amachita kuonetsera kuipa kwawo pomwe ena amachita mwakabisira. Ngakhale zitakhala kuti anthu oterewa sanatichitire zoipa mwachindunji, zochita zawo zimatikhudzabe ndithu. Mwachitsanzo, timakhumudwa komanso timachita mantha tikamva za zinthu zimene anthu oipa achitira achikulire, ana komanso osauka. Anthu oipa amasonyeza mtima wauchinyama ndiponso wauchiwanda. (Yak. 3:15) Komabe anthu a Mulungufe timadziwa kuti pali uthenga wabwino. w17.04 10 ¶4

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena