Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 88-97
  • September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Lamlungu, September 1
  • Lolemba, September 2
  • Lachiwiri, September 3
  • Lachitatu, September 4
  • Lachinayi, September 5
  • Lachisanu, September 6
  • Loweruka, September 7
  • Lamlungu, September 8
  • Lolemba, September 9
  • Lachiwiri, September 10
  • Lachitatu, September 11
  • Lachinayi, September 12
  • Lachisanu, September 13
  • Loweruka, September 14
  • Lamlungu, September 15
  • Lolemba, September 16
  • Lachiwiri, September 17
  • Lachitatu, September 18
  • Lachinayi, September 19
  • Lachisanu, September 20
  • Loweruka, September 21
  • Lamlungu, September 22
  • Lolemba, September 23
  • Lachiwiri, September 24
  • Lachitatu, September 25
  • Lachinayi, September 26
  • Lachisanu, September 27
  • Loweruka, September 28
  • Lamlungu, September 29
  • Lolemba, September 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 88-97

September

Lamlungu, September 1

Muwalere [ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.​—Aef. 6:4.

Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kulera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Sal. 127:3) Mosiyana ndi ana a Aisiraeli akale, masiku ano ana a Mboni za Yehova sabadwa ali odzipereka kwa Mulungu. Komanso mwana sakonda Mulungu kapena choonadi chifukwa chongotengera makolo. Kuyambira nthawi imene mwana wabadwa, makolo ayenera kukhala ndi cholinga choti azithandiza mwanayo kuti adzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti munthu amafunika kudzipereka kwa Yehova, kubatizidwa komanso kutumikira Yehovayo mokhulupirika kuti aikidwe chizindikiro choti adzapulumuke. (Mat. 24:13) Ngati ndinu makolo, nanunso mukhoza kusangalala kwambiri ana anu akadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. w18.03 12 ¶16-17

Lolemba, September 2

Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.​—1 Tim. 4:16.

Anthu onse amene ali ndi udindo wopereka malangizo a m’Malemba, kaya m’banja kapena mumpingo, ayenera kutsanzira Yesu. Akamatero amasonyeza kuti akufunitsitsa kuti Mulungu ndi Mwana wake aziwaumba. Pali madalitso ambiri amene tingapeze tikamatsatira malangizo a Mulungu komanso tikamatsanzira Yehova ndi Yesu popereka malangizo. Ubwino wina ndi wakuti m’mabanja ndi mumpingo mumakhala mtendere. Aliyense amaona kuti ndi wotetezeka komanso amazindikira kuti amakondedwa ndiponso amaonedwa kuti ndi wamtengo wapatali. Komatu uku n’kulawa chabe madalitso amene tidzakhale nawo m’tsogolo. (Sal. 72:7) Malangizo amene Yehova amatipatsa masiku ano amatiphunzitsa mmene tingakhalire mwamtendere mpaka kalekale. Pa nthawiyo tizidzakhala ngati banja logwirizana loyang’aniridwa ndi Atate wachikondi. (Yes. 11:9) Tikakhala ndi maganizo amenewa pa nkhani ya malangizo a Yehova sitidzakayikira mfundo yakuti Mulungu amatilangiza chifukwa chotikonda. w18.03 26 ¶15; 27 ¶17, 19

Lachiwiri, September 3

Iye anali kuwabatiza mumtsinje wa Yorodano, ndipo anthuwo anali kuulula machimo awo poyera.—Mat. 3:6.

Yohane ankabatiza anthu amene ankafuna kusonyeza kuti alapa machimo awo amene anachita polephera kutsatira Chilamulo cha Mose. (Mat. 3:1-6) Koma munthu wofunika kwambiri amene Yohane anabatiza sanabatizidwe chifukwa chofuna kulapa machimo. Yohane anali ndi mwayi wapadera wobatiza Yesu, yemwe ndi Mwana wangwiro wa Mulungu. (Mat. 3:13-17) Yesu sanachimwepo choncho sankafunika kulapa. (1 Pet. 2:22) Koma ubatizo wake unkasonyeza kuti wadzipereka kuti azichita zimene Mulungu amafuna. (Aheb. 10:7) Pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake padzikoli, ophunzira ake ankabatizanso anthu. (Yoh. 3:22; 4:1, 2) Mofanana ndi anthu amene Yohane anabatiza, anthuwa anabatizidwa pofuna kusonyeza kuti alapa machimo awo amene anachita polephera kutsatira Chilamulo cha Mose. Koma Yesu atamwalira n’kuukitsidwa, anthu ankabatizidwa pa chifukwa china. w18.03 5 ¶6-7

Lachitatu, September 4

Munthu wauzimu amafufuza zinthu zonse.​—1 Akor. 2:15.

Kodi kukhala munthu wauzimu kumatanthauza chiyani? Mosiyana ndi munthu wakuthupi, munthu wauzimu amaganizira kwambiri za ubwenzi wake ndi Mulungu. Amayesetsanso kuti ‘azitsanzira Mulungu.’ (Aef. 5:1) Apa tikutanthauza kuti amayesetsa kudziwa maganizo a Mulungu n’kumaona zinthu mmene Mulunguyo amazionera. Amadalira kwambiri Mulungu ndipo amayesetsa kutsatira mfundo zake pa zonse zimene amachita. (Sal. 119:33; 143:10) Munthu wotereyu sachita “ntchito za thupi” koma amakhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Kuti timvetse nkhaniyi tiyeni tiyerekezere chonchi: Munthu amene ali ndi luso pochita bizinezi anthu amangomunena kuti wabizinezi. N’chimodzimodzi ndi munthu amene amaganizira kwambiri zinthu zauzimu kapena kuti zokhudza kulambira Mulungu. Amatchedwa munthu wauzimu. w18.02 19 ¶3, 6

Lachinayi, September 5

Iwe Danieli, munthu wokondedwa kwambiri.​—Dan. 10:11.

Danieli anali ku ukapolo mumzinda wa Babulo, womwe anthu ake ankalambira mafano komanso kuchita zamatsenga. Ndipo Ababulo ankanyoza Ayuda komanso Mulungu wawo Yehova. (Sal. 137:1, 3) Zimenezi ziyenera kuti zinkapweteka kwambiri Danieli komanso Ayuda ena okhulupirika. Danieli ndi anzake ankauzidwa zimene ayenera kudya ndipo zimenezi zinali zovuta chifukwa Danieli sankafuna ‘kudzidetsa ndi zakudya zabwino za mfumu.’ (Dan. 1:5-8, 14-17) Chinthu china chimene chikanasokoneza Danieli chinali maluso ake omwe anachititsa kuti alandire udindo wapadera. (Dan. 1:19, 20) Koma m’malo mokhala wonyada komanso womva zake zokha, Danieli anakhalabe wodzichepetsa ndipo nthawi zonse ankalemekeza Yehova. (Dan. 2:30) Ndipotu Danieli anali adakali wachinyamata pamene Yehova anachititsa kuti atchulidwe limodzi ndi Nowa komanso Yobu monga chitsanzo cha munthu wolungama. (Ezek. 14:14) Kodi Yehova analakwitsa pokhulupirira Danieli chonchi? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti Danieli anakhalabe wokhulupirika komanso womvera mpaka mapeto a moyo wake. w18.02 5 ¶11-12

Lachisanu, September 6

Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake.​—Luka 5:29.

Yesu ankaona zosangalatsa moyenerera. Nthawi ina anapita ‘kuphwando la ukwati’ ndipo nthawi inanso anapita ‘kuphwando lalikulu.’ (Yoh. 2:1-10) Paphwando la ukwatilo, vinyo anatha ndipo iye anasandutsa madzi kukhala vinyo. Komabe sikuti Yesu ankangokhalira kuchita zosangalatsa. Iye ankaika zofuna za Yehova pamalo oyamba ndipo ankadzipereka kwambiri pothandiza anthu ena. Analoleranso kufa imfa yopweteka kwambiri n’cholinga choti anthu adzakhale ndi moyo wosatha. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba.” (Mat. 5:11, 12) Ngati timakondadi Mulungu tidzayesetsa kupewa zinthu zimene amadana nazo, komanso zimene tikungoganiza kuti zingamukhumudwitse.​—Mat. 22:37, 38. w18.01 26 ¶16-18

Loweruka, September 7

Ngati munthu akusasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana, akadzakula adzakhala wosayamika.—Miy. 29:21.

Timapereka zinthu kwa Yehova chifukwa chomukonda komanso kuyamikira zimene watichitira. Tikaganizira zonse zimene Yehova watichitira, timakhudzidwa kwambiri. Mfumu Davide anafotokoza zinthu zimene zinkafunika kuti amange kachisi. Pofotokoza zinthuzi ananena kuti zonse zimene tili nazo n’zochokera kwa Yehova choncho chilichonse chimene tingapereke n’chochokera kwa iyeyo. (1 Mbiri 29:11-14) Kupereka zinthu kumatithandiza. Ndi bwino kuti tikhale ndi mtima wopatsa osati kumangofuna kuti anthu azitipatsa zinthu. Mwachitsanzo, mwana wamng’ono angapatse makolo ake mphatso imene wagula ndi kandalama kamene makolowo anamupatsa. Makolowo akhoza kuyamikira kwambiri. Kapena mwina wachinyamata amene adakali pakhomo ndipo akuchita upainiya angapatse makolo ake ndalama zinazake pothandiza kugula zinthu zina zofunika. N’kutheka kuti makolowo sayembekezera kuti mwana wawo azichita zimenezi. Koma akhoza kulandira mphatsoyi chifukwa chodziwa kuti ndi njira imene mwanayo akuyamikirira zimene amamuchitira. Nayenso Yehova amadziwa kuti kupereka zinthu zathu zamtengo wapatali kumatithandiza. w18.01 18 ¶4, 6

Lamlungu, September 8

Inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.​—Deut. 30:19.

Kungouza ana anu kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika si kokwanira. Ndi bwino kuwathandiza kuganizira mafunso monga akuti: ‘N’chifukwa chiyani Baibulo limatsutsa zinthu zimene thupi lathu limalakalaka? N’chiyani chikunditsimikizira kuti kutsatira mfundo za m’Malemba kungandithandize kuti zinthu zizindiyendera bwino?’ (Yes. 48:17, 18) Mwana amene akufuna kubatizidwa ayenera kuthandizidwa kuti aganizire bwino zinthu zina. Ayenera kuganizira udindo umene munthu amakhala nawo akabatizidwa. Ayeneranso kuona zinthu zabwino zimene angapeze komanso mavuto amene angakumane nawo. Ndiyeno ayenera kuyerekezera zinthu ziwirizi n’cholinga choti aone kuti ubwinowo ndi waukulu kwambiri kuposa mavuto amene angakumane nawo. (Maliko 10:29, 30) Kuganizira mfundo zimenezi munthu asanabatizidwe n’kofunika chifukwa chakuti n’zimene zingamuthandize akadzabatizidwa. Mwana akathandizidwa kuganizira mfundozi akhoza kukhutira ndi zimene amakhulupirira. Iye sangakayikire kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza nthawi zonse. w17.12 21-22 ¶14-15

Lolemba, September 9

Amaziitana potchula iliyonse dzina lake.—Yes. 40:26.

Ena mwa abale ndi alongo athu akuvutika ndi matenda aakulu. Ena ndi achikulire koma akusamaliranso achibale awo okalamba. Ena amavutika kwambiri kuti apeze zinthu zofunika pa moyo. Ndipo ena ali ndi mavuto ngati amene tatchulawa, osati limodzi koma angapo. Ngati Yehova amachita chidwi ndi zinthu zopanda moyo zimene analenga, kuli bwanji inuyo? Mumamutumikira chifukwa choti mumamukonda, osati chifukwa chakuti munalengedwa m’njira yoti muzingochita zimenezo. (Sal. 19:1, 3, 14) Atate wathu wakumwamba amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo. Paja Baibulo limanena kuti ngakhale ‘tsitsi lenilenilo la m’mutu mwathu amaliwerenga.’ (Mat. 10:30) Wolemba masalimo amatitsimikiziranso kuti: “Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa.” (Sal. 37:18) Iye amaona mavuto amene tikukumana nawo ndipo amatha kutipatsa mphamvu kuti tipirire. w18.01 7 ¶1; 8 ¶4

Lachiwiri, September 10

Tabita, dzuka!​—Mac. 9:40.

Petulo ataukitsa Tabita, anthu anadabwa kwambiri moti ambiri “anakhala okhulupirira mwa Ambuye.” Zimenezi zinawalimbikitsa kuti azilalikira za Yesu komanso kuuza anthu kuti Mulungu ali ndi mphamvu youkitsa akufa. (Mac. 9:36-42) Mu nthawi ya Paulo anthu ena anaonanso munthu akuukitsidwa. Tsiku lina, mtumwi Paulo anali pamsonkhano umene unkachitika m’chipinda cham’mwamba ku Torowa, komwe panopa ndi kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Turkey. Paulo anakamba nkhani mpaka pakati pa usiku ndipo mnyamata wina dzina lake Utiko ankamvetsera atakhala pafupi ndi windo m’chipinda chachitatu m’mwamba. Kenako iye anayamba kugona ndipo anagwa kuchoka pawindopo kufika pansi. N’kutheka kuti Luka, yemwe anali dokotala, ndi amene anayamba kufika pamene mnyamatayo anagwera ndipo atamuona ananena kuti sikuti wangokomoka koma wafa. Zitatero, Paulo anatsika masitepe n’kukumbatira thupi la mnyamatayo kenako n’kunena kuti: “Ali moyo tsopano.” Zimenezi ziyenera kuti zinadabwitsa anthu. Iwo ataona kuti mnyamata amene anafayo wauka “anatonthozedwa kwambiri.”​—Mac. 20:7-12. w17.12 5 ¶10-11

Lachitatu, September 11

Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova.​—Sal. 46:8.

Kodi n’zoona kuti anthu ayamba kutulukira njira zothetsera mavuto amene akhala akuwasowetsa mtendere? Ayi si zoona chifukwa sanasiyebe kumenyana. Komanso uchigawenga monga wa pa intaneti, nkhanza za m’banja komanso zinthu zina zaupandu zikuchulukirachulukira. Nawonso matenda oopsa akuwonjezeka. Masiku ano anthu ambiri amene ali ndi maudindo m’boma kapena pa nkhani zamalonda ndi odzikonda. Choncho sangathetse nkhondo, uchigawenga, matenda komanso umphawi. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto amenewa. Taganizirani zimene Yehova adzachitire anthu. Nkhondo: Ufumu wa Mulungu udzathetsa zinthu zimene zimayambitsa nkhondo monga kudzikonda, chinyengo, mtima wokonda dziko lako, chipembedzo chonyenga komanso Satana weniweniyo. (Sal. 46:9) Uchigawenga: Ufumu wa Mulungu wayamba kale kuphunzitsa anthu kuti azikondana komanso kukhulupirirana ndipo palibe boma lina lililonse limene lingachite zimenezi. (Yes. 11:9) Matenda: Yehova adzathandiza anthu ake kuti asamadwale. (Yes. 35:5, 6) Umphawi: Yehova adzathetsa umphawi ndipo adzapereka zinthu zonse zofunika kuti anthu ake akhale ndi moyo wabwino komanso akhale naye pa ubwenzi wolimba.​—Sal. 72:12, 13. w17.11 24 ¶14-16

Lachinayi, September 12

Kuti musakhale ndi mlandu wa magazi.​—Deut. 19:10.

Cholinga chachikulu cha mizinda yothawirako chinali kuteteza Aisiraeli kuti asakhale ndi mlandu wamagazi. Yehova amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali choncho amadana ndi “manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.” (Miy. 6:16, 17) Mulungu ndi wolungama komanso woyera moti sangalekerere mlandu wopha munthu, ngakhale zitachitika mwangozi. Mosiyana ndi Yehova, alembi ndi Afarisi sankalemekeza moyo. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anawauza kuti: “Munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu. Inuyo simunalowemo, ndipo ofuna kulowamo munawatsekereza.” (Luka 11:52) Iwo anali ndi udindo wothandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu komanso wowathandiza kuti aziyenda pamsewu wopita ku moyo wosatha. Koma m’malo mochita zimenezi, anachititsa kuti anthu asamatsatire “Mtumiki Wamkulu wa moyo,” koma aziyenda pamsewu wopita kukawonongedwa. (Mac. 3:15) Alembi ndi Afarisi anali onyada komanso odzikonda ndipo sankasamala za anthu ena. Iwo anali oipa mtima kwambiri komanso opanda chifundo. w17.11 15-16 ¶9-10

Lachisanu, September 13

Aliyense wochita manyazi ndi ine, . . . Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi.”​—Maliko 8:38.

Mwina poyamba sitinafotokozere achibale athu kuti tayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Koma chikhulupiriro chathu chitayamba kukula tinaona kuti ndi bwino kuuza ena zimene tayamba kukhulupirira. Koma mwina kukhala wokhulupirika kwa Yehova kwachititsa kuti muzisiyana maganizo ndi achibale anu omwe si Mboni.Ngati zili choncho, muziyesetsa kuwamvetsa. Ifeyo tikhoza kusangalala kwambiri kuti taphunzira mfundo zolondola za m’Baibulo koma achibale athu akhoza kuganiza kuti tikupusitsidwa kapena talowa gulu lolakwika. Akhoza kuganizanso kuti tasiya kuwakonda chifukwa choti tasiya kuchita nawo zikondwerero zina. Atha kumaonanso kuti tsogolo lathu silili bwino. Choncho kuti tiziwamvetsa, tiyenera kuyesetsa kuona zinthu mmene iwo akuzionera komanso kuwamvetsera bwino kuti tidziwe zimene zikuwadetsa nkhawa. (Miy. 20:5) Mtumwi Paulo ankayesetsa kumvetsa “anthu osiyanasiyana” n’cholinga choti akwanitse kuwauza uthenga wabwino, ndipo njira imeneyi ingatithandizenso ifeyo.​—1 Akor. 9:19-23. w17.10 15 ¶11-12

Loweruka, September 14

Muimbireni [Yehova] nyimbo zomutamanda.​—Sal. 33:2.

Mwina sitikonda kuimba mokweza chifukwa choganiza kuti sititha kuimba. Koma tikhoza kuphunzira kuimba ngati titatsatira mfundo zingapo. Kapumidwe kabwino kamathandiza kuti munthu aziimba mokweza komanso mwamphamvu. Mpweya ndi umene umathandiza munthu kuti alankhule kapena kuimba bwino ndipo izi tingaziyerekezere ndi mmene magetsi amathandizira kuti mababu aziwala. Choncho mukamaimba, muzikweza mawu mmene mumalankhulira mwinanso kuposa pamenepo. Ndipotu malemba ena amatilimbikitsa kuti ‘tizifuula mosangalala’ poimbira Yehova. (Sal. 33:1-3)Tayesani kuchita izi: Sankhani nyimbo yomwe imakusangalatsani kwambiri m’buku lathu la nyimbo. Werengani mawu ake mokweza komanso mwamphamvu. Kenako tchulani mawu amumzere winawake ndi mphamvu yomweyo koma popanda kupumira. Kenako imbani mawu amumzerewo mwamphamvu komanso mokweza. (Yes. 24:14) Mukatero mudzatha kuimba mokweza ndipo simuyenera kuchita mantha kapena manyazi. w17.11 5-6 ¶11-13

Lamlungu, September 15

Aliyense amene Mulungu woona analimbikitsa mtima wake, ananyamuka kuti apite kukamanganso nyumba ya Yehova, yomwe inali ku Yerusalemu.​—Ezara 1:5.

Pa ulendowo Ayuda ayenera kuti ankaganizira kwambiri za mmene zinthu zidzakhalire ku Yerusalemu. Iwo anali atamva kale kwa achikulire kuti mzindawu unali wokongola kwambiri komanso kuti kachisi anali waulemerero. (Ezara 3:12) Kodi mukanakhala nawo pa ulendowu mukanamva bwanji mutaona Yerusalemu koyamba? Muyenera kuti mukanamva chisoni poona mmene mzindawu wawonongekera n’kungokhala tchire lokhalokha. Mwina mukanaona kuti mpanda wake ndi wosiyana kwambiri ndi mpanda wolimba wa ku Babulo chifukwa unali utagumukagumuka. Ngakhale zinali choncho, anthuwo sanataye mtima. Iwo anali ataona kale Yehova akuwathandiza pa ulendo wawo wautali wobwerera ku Yerusalemu. Atangofika, anakonza guwa lansembe pamalo pamene panali kachisi ndipo anayamba kupereka nsembe kwa Yehova tsiku lililonse.​—Ezara 3:1, 2. w17.10 26-27 ¶2-3

Lolemba, September 16

Usaope kapena kuchita mantha chifukwa Yehova . . . ali ndi iwe.​—1 Mbiri 28:20.

Solomo ayenera kuti anaphunzira zambiri kwa bambo ake pa nkhani yolimba mtima. Davide anasonyeza kulimba mtima pokamenyana ndi Goliati yemwe anali chimphona chodziwa nkhondo. Mulungu anathandiza Davide moti anapha Goliati pogwiritsa ntchito mwala umodzi wokha. (1 Sam. 17:45, 49, 50) M’pomveka kuti Davide anauza Solomo kuti alimbe mtima n’kumanga kachisi. Anamuuzanso kuti Yehova akhala naye mpaka ntchito yonse yomanga kachisiyo itatha. Solomo ayenera kuti ankaganizira kwambiri mawu amenewa ndipo anamuthandiza kuti asamadziderere chifukwa choti anali wamng’ono komanso wosadziwa zambiri. Iye analimba mtima n’kuyamba ntchitoyo ndipo Yehova anamuthandiza kuti amalize kumanga kachisi wokongolayo m’zaka 7 ndi hafu zokha. Yehova angatithandizenso kuti tizichita zinthu molimba mtima n’kukwaniritsa ntchito yathu m’banja komanso mumpingo. (Yes. 41:10, 13) Tisamakayikire kuti tikakhala olimba mtima polambira Yehova, iye adzatidalitsa panopa komanso m’tsogolo. w17.09 28-29 ¶3-4; 32 ¶20-21

Lachiwiri, September 17

Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.​—Aheb. 4:12.

Anthu a Mulungufe sitikayikira zoti mawu amene Mulungu amatiuza “ndi amoyo ndi amphamvu.” Ambirife mphamvu ya Baibulo yatithandiza kusintha kwambiri moyo wathu. Abale ndi alongo ena m’mbuyomo anali akuba, ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena anali achiwerewere. Anthu ena ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino m’dzikoli koma mumtima mwawo ankaona kuti akusowa chinachake. (Mlal. 2:3-11) Mphamvu ya Baibulo yathandiza anthu ambiri amene anataya mtima kuti ayambe kuyenda panjira ya ku moyo. Mwina inuyo mwawerengapo za anthu amene anasintha kwambiri moyo wawo munkhani za mu Nsanja ya Olonda zakuti “Baibulo Limasintha Anthu.” Mwaonanso kuti Malemba amathandizabe Akhristu amene anabatizidwa kuti apitirize kusintha moyo wawo. w17.09 23 ¶1

Lachitatu, September 18

Mwa chifundo cha Yehova pa iye, . . . [anawatulutsa] kukawasiya kunja kwa mzinda.​—Gen. 19:16.

Nkhani ya Lotiyi ikusonyeza kuti Yehova amadziwa bwino mavuto amene atumiki ake okhulupirika amakumana nawo. (Yes. 63:7-9; Yak. 5:11; 2 Pet. 2:9) Yehova amaphunzitsanso anthu ake kuti azikhala achifundo. Chitsanzo ndi lamulo limene anapatsa Aisiraeli pa nkhani yolanda munthu chovala chake kuti chikhale chikole. (Eks. 22:26, 27) Munthu wopanda chifundo akhoza kulanda chofunda cha munthu amene ali ndi ngongole n’kumusiya kuti agone osafunda. Koma Yehova sankafuna kuti anthu ake azikhala oipa mtima choncho. Ankafuna kuti azikhala achifundo. Kodi tikuphunzira chiyani pa lamulo limeneli? Tikadziwa vuto limene m’bale wathu ali nalo, lomwe tikhoza kuthandizapo, si bwino kungomusiya chifukwa zingakhale ngati tamusiya kuti agone osafunda.​—Akol. 3:12; Yak. 2:15, 16; 1 Yoh. 3:17. w17.09 9 ¶4-5

Lachinayi, September 19

Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa chimene akuchita.—Luka 23:34.

Yesu anapemphera kuti Atate wake akhululukire anthu amene amukhomera pamtengowo. Apatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kufatsa komanso kuleza mtima ngakhale zinthu zitavuta kwambiri. (1 Pet. 2:21-23) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ofatsa komanso oleza mtima? Paulo ananena njira imodzi imene tingachitire zimenezi pamene anauza Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Akol. 3:13) Koma kunena zoona, pamafunika kufatsa komanso kuleza mtima kuti titsatire lamulo limeneli. Koma tikamakhululukira anzathu timathandiza kuti mumpingo mukhale mgwirizano. Mkhristu aliyense ayenera kukhala wofatsa komanso woleza mtima. Zili choncho chifukwa chakuti popanda kuchita zimenezi sangadzapulumuke. (Mat. 5:5; Yak. 1:21) Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikakhala ndi makhalidwe amenewa timalemekeza Yehova komanso timathandiza ena kuti azitsatira malangizo a m’Baibulo.​—Agal. 6:1; 2 Tim. 2:24, 25. w17.08 25-26 ¶15-17

Lachisanu, September 20

Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.​—2 Pet. 2:9.

M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti Yehova amachita zinthu zosayembekezereka. Mwachitsanzo, Hezekiya anali mfumu pa nthawi imene Senakeribu, yemwe anali mfumu ya Asuri, analanda mizinda yonse yokhala ndi mipanda ya ku Yuda, kupatulapo Yerusalemu. (2 Maf. 18:1-3, 13) Kenako Senakeribu ankafuna kuti alandenso Yerusalemu. Kodi Hezekiya anachita chiyani pa nthawi yovutayi? Iye anapemphera kwa Yehova komanso anafunsira nzeru kwa mneneri Yesaya. (2 Maf. 19:5, 15-20) Hezekiya anasonyezanso kuti si wamakani chifukwa anapereka ndalama zimene Senakeribu analamula. (2 Maf. 18:14, 15) Iye anachitanso zinthu zina pokonzera nthawi imene mzinda wa Yerusalemu udzazunguliridwe ndi Asuri. (2 Mbiri 32:2-4) Koma kodi nkhaniyi inatha bwanji? Yehova anatumiza mngelo yemwe anapha asilikali a Senakeribu okwana 185,000 usiku umodzi. Apatu Yehova anachita zinthu zimene ngakhale Hezekiya sankayembekezera.​—2 Maf. 19:35. w17.08 10 ¶7; 11 ¶12

Loweruka, September 21

Mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.​—Mat. 28:19, 20.

Kodi inuyo mungakonzekere bwanji kuti mudzachite utumiki wa nthawi zonse? Chofunika kwambiri ndi kukhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Yehova. Choncho muyenera kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, kusinkhasinkha tanthauzo lake komanso kufotokoza zimene mumakhulupirira pa misonkhano. Pa nthawi imene muli pa sukulu mukhoza kuphunzira njira zolalikirira mwaluso. Muziyesetsa kuchita chidwi ndi anthu powafunsa maganizo awo komanso kuwamvetsera akamayankha. Muzidziperekanso kugwira nawo ntchito zina mumpingo monga kuyeretsa ndi kukonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu. Yehova amagwiritsa ntchito anthu odzichepetsa komanso odzipereka. (Sal. 110:3; Mac. 6:1-3) Kumbukirani kuti mtumwi Paulo anatenga Timoteyo kuti azichita naye umishonale chifukwa choti abale “anamuchitira umboni wabwino.”​—Mac. 16:1-5. w17.07 23-24 ¶7; 26 ¶14

Lamlungu, September 22

Bondo lililonse lidzagwadira ine ndipo lilime lililonse lidzalumbira kwa ine.​—Yes. 45:23.

Ngati nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova singathetsedwe m’maganizo mwa anthu kapena angelo, pazikhalabe kusagwirizana kwa mayiko, mitundu, mafuko, mabanja komanso anthu. Koma Yehova akadzasonyeza zoti ndi woyenera kulamulira, aliyense azidzamvera ulamuliro wake wachilungamo ndipo padzakhala mtendere m’chilengedwe chonse. (Aef. 1:9, 10) Posachedwapa, Yehova adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira ndipo ulamuliro wa Satana ndiponso wa anthu udzaonekeratu kuti ndi wolephera ndipo udzachotsedwa. Ufumu wa Mesiya udzasonyeza kuti ulamuliro wa Mulungu ndi wabwino ndipo anthu amene adzakhalebe okhulupirika adzasonyeza kuti n’zotheka kukhalabe kumbali ya ulamuliro wa Mulungu. (Yes. 45:24) Kodi inuyo mukufuna kukhala m’gulu la anthu osonyeza kuti ulamuliro wa Yehova ndi wabwino? Mosakayikira mwayankha kale kuti inde. Koma kuti tikhalebe okhulupirika tiyenera kumaona kuti nkhani ya ulamuliroyi ndi yofunika kwambiri. w17.06 23 ¶4-5

Lolemba, September 23

Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.​—Miy. 17:17.

Anthu amamva chisoni mosiyanasiyana. Choncho ndi bwino kupitiriza kulimbikitsa munthu ngakhale achibale kapena anzake amene ankamulimbikitsa pa nthawi ya maliro atachoka. Abale ndi alongo ayenera kulimbikitsa munthu mpaka nthawi imene chisoni chake chachepa. (1 Ates. 3:7) Tizikumbukira kuti anthu oferedwa akhoza kumvanso chisoni pa nthawi inayake pa chaka, akamva nyimbo inayake, kuona zithunzi, kuchita zinthu zina komanso akamva fungo kapena phokoso linalake. Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira angavutike kwambiri akayambiranso kuchita zinthu zina payekha monga kupita kumsonkhano kapena ku Chikumbutso. Koma tizikumbukiranso kuti anthu amene aferedwa amafunikira kuwalimbikitsa nthawi zonse, osati pa nthawi zapadera zokha. w17.07 16 ¶17-19

Lachiwiri, September 24

Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.​—Afil. 2:4.

Chochititsa chidwi n’chakuti tikamathandiza ena timaiwala mavuto athu komanso timasiya kudandaula. Alongo onse, kaya ali pa banja kapena ayi, akhoza kukhala osangalala akakhala antchito anzake a Mulungu n’kumalalikira uthenga wabwino. Cholinga chawo chimakhala kulemekeza Mulungu n’kumachita zimene amafuna. Ena amafika poona kuti kulalikira kuli ngati mankhwala awo. Tonsefe tingathandize kuti mpingo ukhale wogwirizana ngati timaganizira abale ndi alongo athu komanso anthu a m’gawo lathu. Mtumwi Paulo ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye ankasamalira Akhristu a ku Tesalonika ngati mmene “mayi woyamwitsa” amachitira posamalira mwana wake. Iye analinso ngati bambo wawo. (1 Ates. 2:7, 11, 12) Ana akaphunzitsidwa bwino n’kuyamba kukonda Yehova komanso kutsatira malangizo ake, amalimbikitsa anthu a m’banja lawo. Iwo amalemekeza makolo awo komanso kuwathandiza m’njira zina. Amawathandizanso pa nkhani zokhudza kulambira. w17.06 7 ¶13-14; 8 ¶17

Lachitatu, September 25

Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama.—Luka 16:9.

Tonse tikudziwa kuti pali anthu mabiliyoni ambiri amene ndi osauka kwambiri pomwe ena ali ndi chuma choti anthu ambiri sangachimalize pa moyo wawo wonse. Yesu ankadziwa kuti zinthu sizingayende mwachilungamo pa nkhani zachuma mpaka Ufumu wa Mulungu udzabwere. Dziko la Satanali lili ndi mbali zitatu zikuluzikulu. Pali andale, achipembedzo komanso “amalonda,” amene amatchulidwa pa Chivumbulutso 18:3. Anthu a Mulungu amapeweratu ndale ndiponso chipembedzo chonyenga koma ambiri sangapeweretu zamalonda m’dzikoli. Akhristufe tingachite bwino kudzifufuza pa nkhani ya malondayi podzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji chuma changa posonyeza kuti ndine wokhulupirika kwa Mulungu? Nanga ndingapewe bwanji kuchita kwambiri zamalonda? Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti anthu a Mulungu amamudalira kwambiri m’masiku ovuta ano?’ w17.07 7-8 ¶1-3

Lachinayi, September 26

Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo.—Luka 21:34.

Yesu ankadziwa kuti munthu akhoza kusokonezeka chifukwa chodera nkhawa zinthu za m’dzikoli. Mufanizo lake la munthu wofesa mbewu, Yesu ananena kuti anthu ena akhoza kumva “mawu a ufumu” n’kuyamba kuwatsatira koma “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” chimalepheretsa mawuwo kukula. (Mat. 13:19-22; Maliko 4:19) Choncho tikapanda kusamala, nkhawa za tsiku ndi tsiku zikhoza kusokoneza mtima wathu n’kuyamba kufooka. Mofanana ndi Petulo, tingasonyeze kuti timakonda Khristu ngati tiika ntchito yolalikira pamalo oyamba. Koma kodi tingatani kuti tisasiye kuchita zimenezi? Nthawi zina tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimasangalala kwambiri ndikamachita zinthu ziti, zokhudza kutumikira Yehova kapena zina?’ w17.05 23 ¶3-4

Lachisanu, September 27

[Muzilankhula] zomveka ndi lilime lanu.​—1 Akor. 14:9.

Ngati anthu asamukira m’dziko lina ndipo mulibe mpingo wachilankhulo chawo, ayenera kusonkhana mumpingo wachilankhulo cha dzikolo. (Sal. 146:9) Koma ngati mpingo wachilankhulo chanu ukupezeka, ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi tiyenera kukhala mumpingo wachilankhulo chiti? M’bale asanasankhe zochita, ayenera kuiganizira bwino nkhaniyi, kuipempherera komanso kukambirana ndi banja lake lonse. (1 Akor. 11:3) Makolo ayenera kuganizira bwino zimene ana awo akufunikira. N’zoona kuti mwana sangaphunzire mokwanira zokhudza Yehova pa nthawi yochepa imene amakhala pamisonkhano mlungu uliwonse. Komabe ana akamapita kumisonkhano imene imachitika m’chilankhulo chimene amachidziwa bwino akhoza kuphunzira zambiri, mwina kuposa zimene makolo awo angaganizire. Izi sizingachitike ngati ana sakudziwa bwino chilankhulo cha mpingo umene amasonkhana.​—1 Akor. 14:11. w17.05 10 ¶10-11

Loweruka, September 28

Chifukwa cha kudzipereka mwaufulu kwa anthu, tamandani Yehova.​—Ower. 5:2.

Tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndili ndi chikhulupiriro cholimba moti ndimagwiritsa ntchito zinthu zimene ndili nazo kuti nditumikire Yehova? Ngati ndikufuna kukasaka ndalama kudziko lina, kodi ndapemphera kwa Yehova n’kuganizira mmene kuchokako kungakhudzire banja langa komanso mpingo?’ Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wosonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Kuyambira nthawi ya Adamu ndi Hava, Satana wakhala akuyesetsa kuti anthu akhale kumbali yake potsutsana ndi Yehova. Choncho tikamatumikira Yehova modzipereka timasonyeza Satana kuti tili kumbali ya Yehovayo. Yehova amasangalala tikamachita zimenezi chifukwa choti tili ndi chikhulupiriro komanso mtima wosagawanika. (Miy. 23:15, 16) Tikamamvera Yehova timathandiza kuti ayankhe Satana amene amamunyoza. (Miy. 27:11) Mwachidule tingati tikamamvera Yehova timakhala kuti tikumupatsa zinthu zamtengo wapatali ndipo amasangalala kwambiri. w17.04 32 ¶15-16

Lamlungu, September 29

Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako, chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa. Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.​—Mlal. 5:4.

Mu Chilamulo cha Mose munali lamulo lakuti: “Munthu akalonjeza kwa Yehova, kapena akachita lumbiro . . . , asalephere kukwaniritsa mawu ake. Achite malinga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake.” (Num. 30:2) Patapita nthawi, Solomo analemba mawu amulemba la leroli. Nayenso Yesu anasonyeza kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu. Anati: “Munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’” (Mat. 5:33) Izi zikusonyeza kuti kulonjeza zinthu kwa Mulungu ndi nkhani yaikulu. Tikutero chifukwa chakuti zimene tingachite pa nkhaniyi, zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova. Davide analemba kuti: “Ndani angakwere m’phiri la Yehova? Ndipo ndani anganyamuke kukalowa m’malo ake opatulika? Aliyense . . . amene sanaone Moyo wanga [wa Yehova] ngati wopanda pake, kapena kulumbira mwachinyengo.”​—Sal. 24:3, 4. w17.04 3-4 ¶3-4

Lolemba, September 30

Iye sanena miseche ndi lilime lake.​—Sal. 15:3.

Mkhristu akaona kuti sanachitiridwe chilungamo ayenera kupewa miseche. N’zoona kuti timafunika kupempha thandizo kwa akulu komanso kuwauza ngati munthu wina wachita tchimo lalikulu. (Lev. 5:1) Koma zinthu zambiri zimene anthu amalakwitsa sizikhala machimo aakulu ndipo zimakhala zotheka kuzithetsa popanda kuuza akulu kapena munthu aliyense. (Mat. 5:23, 24; 18:15) Tiyenera kutsatira mfundo za m’Baibulo pothetsa nkhani zoterezi. Nthawi zina tikhoza kuzindikira kuti amene tinalakwitsa ndi ifeyo poganiza kuti munthu wina anatichitira zinthu zopanda chilungamo. Zikatero tikhoza kusangalala kuti sitinaikulitse nkhaniyo poipitsa mbiri ya Mkhristu mnzathu. Tizikumbukira kuti kaya zimene tikuganizazo n’zoona kapena ayi, kulankhula zoipa za munthuyo, kumangowonjezera mavuto. Ngati ndife okhulupirika kwa Yehova komanso abale athu tidzapewa zimenezi. w17.04 21 ¶14

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena