Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es19 tsamba 77-87
  • August

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • August
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
  • Timitu
  • Lachinayi, August 1
  • Lachisanu, August 2
  • Loweruka, August 3
  • Lamlungu, August 4
  • Lolemba, August 5
  • Lachiwiri, August 6
  • Lachitatu, August 7
  • Lachinayi, August 8
  • Lachisanu, August 9
  • Loweruka, August 10
  • Lamlungu, August 11
  • Lolemba, August 12
  • Lachiwiri, August 13
  • Lachitatu, August 14
  • Lachinayi, August 15
  • Lachisanu, August 16
  • Loweruka, August 17
  • Lamlungu, August 18
  • Lolemba, August 19
  • Lachiwiri, August 20
  • Lachitatu, August 21
  • Lachinayi, August 22
  • Lachisanu, August 23
  • Loweruka, August 24
  • Lamlungu, August 25
  • Lolemba, August 26
  • Lachiwiri, August 27
  • Lachitatu, August 28
  • Lachinayi, August 29
  • Lachisanu, August 30
  • Loweruka, August 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2019
es19 tsamba 77-87

August

Lachinayi, August 1

Osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.​—Mat. 26:39.

Kuti tikhale aphunzitsi abwino, tiyenera kuyamba ifeyo kuphunzira mwakhama. (1 Tim. 4:15, 16) N’chimodzimodzi ndi nkhani yopereka malangizo. Munthu amene ali ndi udindo wopereka malangizo ayenera kuyamba iyeyo kutsatira malangizo a Yehova ndi mtima wonse. Munthu akakhala wodzichepetsa n’kumamvera Yehova amalemekezedwa ndipo amakhala ndi ufulu wolankhula pophunzitsa ena komanso kuwalangiza. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Yesu. Yesu ankamvera Atate wake ngakhale pamene kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri. Iye ankaphunzitsa bwino ndiponso ankachita zinthu mwanzeru koma ankaonetsetsa kuti ulemu wonse ukupita kwa Yehova. (Yoh. 5:19, 30) Popeza Yesu anali wodzichepetsa komanso womvera, anthu amaganizo abwino ankamukonda ndipo iye ankawachitira chifundo komanso kuwaphunzitsa mokoma mtima. (Mat. 11:29) Mawu ake okoma mtima ankalimbikitsa kwambiri anthu amene anali ngati bango lophwanyika komanso nyale yomwe yangotsala pang’ono kuzima. (Mat. 12:20) Yesu ankasonyezabe chikondi ndi kukoma mtima ngakhale pamene anthu achita zinthu zopsetsa mtima. Umboni wake ndi zimene anachita pothandiza atumwi ake omwe ankasonyeza mtima wonyada komanso wofuna maudindo.​—Maliko 9:33-37; Luka 22:24-27. w18.03 26 ¶15-16

Lachisanu, August 2

Chofanana ndi chingalawacho [chimene ndi ubatizo] chikupulumutsanso inuyo tsopano.’—1 Pet. 3:21.

Petulo ankanena za ntchito yomanga chingalawa imene Nowa anagwira. Chingalawa chinali umboni woonekeratu wakuti Nowa anali wodzipereka pochita zimene Mulungu ankafuna. Iye anagwira mokhulupirika ntchito imene Mulungu anamupatsa. Zimene Nowa anachita chifukwa cha chikhulupiriro zinathandiza kuti iye ndi banja lake apulumuke Chigumula. Chingalawa chinali ngati umboni wakuti Nowa anali ndi chikhulupiriro. N’chimodzimodzinso ndi ubatizo. Umakhala ngati umboni wosonyeza kuti munthu wadzipereka kwa Yehova chifukwa choti amakhulupirira Khristu. Mofanana ndi Nowa, anthu amene adzipereka kwa Mulungu amagwira mokhulupirika ntchito imene Mulunguyo wawapatsa. Mofanana ndi Nowa amene anapulumutsidwa pa nthawi ya Chigumula, anthu obatizidwa amene adzakhalebe okhulupirika adzapulumuka pamene dziko loipali lizidzawonongedwa. (Maliko 13:10; Chiv. 7:9, 10) N’chifukwa chake kudzipereka kwa Mulungu komanso kubatizidwa n’kofunika kwambiri. Ndipo munthu amene amazengereza kubatizidwa akhoza kutaya mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. w18.03 4 ¶3-4

Loweruka, August 3

Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.​—Miy. 22:15.

Makolo ena angaganize kuti, ‘Ngati mwana wangayu sabatizidwa ndiye kuti sangachotsedwe.’ N’chifukwa chiyani tinganene kuti makolo oterewa amadzipusitsa? (Yak. 1:22) N’zoona kuti makolo achikhristu sangakonde kuti mwana wawo abatizidwe ali wamng’ono kwambiri moti sangamvetse zimene akuchita podzipereka kwa Mulungu. Koma si nzeru kuganiza kuti mwana amene sanabatizidwe ndiye kuti sangaimbidwe mlandu ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Ubatizo si umene umachititsa kuti munthu aimbidwe mlandu ndi Yehova kapena ayi. Yehova amaona kuti mwana akhoza kuweruzidwa ngati wafika potha kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika. (Yak. 4:17) Choncho m’malo moletsa mwana kuti abatizidwe, makolo anzeru amayesetsa kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Amayesetsa kuthandiza mwana wawo kuti azikonda mfundo zapamwamba za Yehova kuchokera mumtima. (Luka 6:40) Akatero mwanayo amafunitsitsa kuti azitsatira mfundo zachilungamo za Yehova.​—Yes. 35:8. w18.03 11 ¶12-13

Lamlungu, August 4

Nowa anayenda ndi Mulungu woona.​—Gen. 6:9.

Nowa anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zina 350 Chigumula chitachitika. (Gen. 9:28) Nowa analidi chitsanzo chabwino pa nkhani yokhulupirika komanso kumvera. Kuti tikhale okhulupirika ndiponso omvera ngati Nowa, tiyenera kutsatira mfundo zachilungamo za Mulungu, kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba komanso kupewa kukhala mbali ya dziko la Satanali. (Mat. 6:33; Yoh. 15:19) N’zoona kuti zimene timachita pa moyo wathu sizisangalatsa anthu a m’dzikoli. Ndipo kutsatira malamulo a Mulungu pa nkhani zokhudza ukwati ndiponso kugonana kwachititsa kuti anthu a m’mayiko ena afalitse nkhani zoipa zokhudza ifeyo. (Mal. 3:17, 18) Koma mofanana ndi Nowa, timaopa Yehova osati anthu. Timadziwa kuti ndi iye yekha amene amapereka moyo wosatha. (Luka 12:4, 5) Koma kodi inuyo mudzapitiriza ‘kuyenda ndi Mulungu’ ngakhale pamene anthu akukunyozani kapena kukutsutsani? Nanga mutakumana ndi mavuto azachuma, kodi mudzapitiriza kudalira Yehova? Ngati ndinu okhulupirika ndiponso omvera ngati Nowa, simuyenera kukayikira kuti Yehova adzakusamalirani.​—Afil. 4:6, 7. w18.02 4 ¶4, 8; 5 ¶9-10

Lolemba, August 5

Munthu wokonda zinthu za m’dziko [kapena kuti munthu wakuthupi, mawu a m’munsi] salandira zinthu za mzimu wa Mulungu.​—1 Akor. 2:14.

Anthu ambiri m’dzikoli amaganizira kwambiri zofuna zawo. Pofotokoza za maganizo amenewa, Paulo ananena kuti “kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” (Aef. 2:2) Kaganizidweka kamachititsa kuti anthu ambiri azingotengera zimene anzawo akuchita. Iwo amangochita zimene akuona kuti n’zabwino ndipo saganizira mfundo za Mulungu. Munthu wakuthupi amaganizira kwambiri za kutchuka, chuma komanso kulimbana ndi aliyense amene iyeyo akuganiza kuti akumuphwanyira ufulu. Munthu wotereyu amakonda kuchita “ntchito za thupi.” (Agal. 5:19-21) Amachita zinthu monga kulimbikitsa magawano, kutengera anzawo kukhoti, salemekeza anthu amene akuwatsogolera ndiponso amakonda kudya kapena kumwa mopitirira malire. Anthu oterewa akakumana ndi mayesero sachedwa kugonja.​—Miy. 7:21, 22. w18.02 19 ¶3-5

Lachiwiri, August 6

Anthu adzakhala . . . okonda zosangalatsa.​—2 Tim. 3:2, 4.

Kukonda zosangalatsa moyenerera si kulakwa. Sikuti Yehova amafuna kuti tizidzimana chilichonse chosangalatsa. Paja Baibulo limalimbikitsa anthu okhulupirika kuti: “Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala.” (Mlal. 9:7) Lemba la 2 Timoteyo 3:4 limanena za anthu amene sakonda Mulungu koma amakonda zosangalatsa. Onani kuti lembali silinena kuti anthu amakonda zosangalatsa kuposa Mulungu, zomwe zingasonyeze kuti anthuwo amakondabe Mulungu pang’ono. Koma limanena kuti amakonda zosangalatsa “m’malo mokonda Mulungu.” Katswiri wina wa Baibulo analemba kuti lembali “silitanthauza kuti anthuwa amakondanso Mulungu. Koma limatanthauza kuti sakonda Mulungu ngakhale pang’ono.” Ilitu ndi chenjezo lamphamvu kwambiri kwa anthu amene ayamba kukonda kwambiri zosangalatsa. Mawu oti “okonda zosangalatsa” amafotokoza za anthu amene ‘amatengeka ndi zosangalatsa za moyo uno.’​—Luka 8:14. w18.01 25 ¶14-15

Lachitatu, August 7

Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.​—Miy. 3:9.

Yehova amapereka zinthu mowolowa manja moti zonse zimene tili nazo n’zochokera kwa iye. Zinthu zonse zomwe zili padzikoli, monga golide komanso siliva, ndi za Yehova ndipo amazigwiritsa ntchito kuti zinthu zamoyo zipitirize kukhala ndi moyo. (Sal. 104:13-15; Hag. 2:8) Mwachitsanzo, Yehova ankapatsa Aisiraeli mana ndi madzi pa zaka 40 zimene anali m’chipululu moti “sanasowe kanthu.” (Eks. 16:35; Neh. 9:20, 21) Pa nthawi inanso, Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Elisa kuti achulukitse mafuta ochepa amene mkazi wina wamasiye anatsala nawo. Zimene Mulungu anamuchitirazi zinamuthandiza kuti apeze ndalama zobwezera ngongole zake komanso zoti iyeyo ndi mwana wake azigwiritsa ntchito. (2 Maf. 4:1-7) Yehova anagwiritsanso ntchito Yesu kuti athandize anthu kupeza chakudya komanso ndalama. (Mat. 15:35-38; 17:27) Yehova ali ndi zinthu zambiri zimene angazigwiritse ntchito kuti zinthu ziziyenda bwino padzikoli. Koma amafunabe kuti atumiki ake azipereka zinthu zawo kuti zizithandiza pa ntchito ya gulu lake.​—Eks. 36:3-7. w18.01 17-18 ¶1-3

Lachinayi, August 8

Tsopano chotsani moyo wanga Yehova.​—1 Maf. 19:4.

Baibulo limasonyeza kuti m’mbuyomu anthu ena amene ankatumikira Mulungu mokhulupirika ankamva kuti sangapirire mavuto awo. (Yobu 7:7) Koma m’malo motaya mtima, iwo ankadalira Yehova kuti awapatse mphamvu. Ndipo sanagwiritsidwe mwala chifukwa Mulungu wathu “amapereka mphamvu kwa munthu wotopa.” (Yes. 40:29) Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anthu a Mulungu ena akakumana ndi mavuto amasiya kuchita zinthu zokhudza kulambira. Iwo amaona kuti zinthu zimenezo n’zimene zikuwapanikiza, osati kuwabweretsera madalitso. Amasiya kuwerenga Mawu a Mulungu, kupezeka pamisonkhano ndiponso kulalikira. Koma vuto ndi lakuti zimene akuchitazo n’zimene Satana amafuna. Mdyerekezi safuna kuti tizichita khama pa zinthu zokhudza kulambira chifukwa amadziwa kuti zinthu zimenezo zingatipatse mphamvu. Choncho mukatopa kwambiri ndi mavuto enaake, musamasiye kuchita zinthu zokhudza kulambira Yehova. M’malomwake muziyesetsa kumuyandikira ndipo iye “adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”​—1 Pet. 5:10; Yak. 4:8. w18.01 7-8 ¶2-3

Lachisanu, August 9

Yehova ndi . . . wotsitsira Kumanda, ndiponso woukitsa.​—1 Sam. 2:6.

Nkhani yachiwiri inachitika nthawi ya Elisa, yemwe analowa m’malo mwa Eliya. Mkazi wina wachiisiraeli, yemwe anali wodziwika ku Sunemu, analandira bwino Elisa m’nyumba yake. Yehova anadalitsa mkaziyo ndi mwamuna wake wachikulire moti anakhala ndi mwana wamwamuna. Koma patapita zaka zingapo, mwanayo anamwalira. Kodi inuyo mukuganiza kuti mayi ake anamva bwanji? Iye atakambirana ndi mwamuna wake, ananyamuka ulendo wa makilomita 30 kupita kukaonana ndi Elisa kuphiri la Karimeli. Mneneriyo anatuma Gehazi kuti atsogole popita ku Sunemu n’cholinga choti akaukitse mwanayo koma sanathe kumuukitsa. Kenako mayi a mwanayo anafika limodzi ndi Elisa kunyumbako. (2 Maf. 4:8-31) Elisa anafika pafupi ndi thupi la mwanayo n’kupemphera. Mnyamatayo anauka ndipo anamupereka kwa mayi ake omwe anasangalala kwambiri. (2 Maf. 4:32-37) Ku Sunemu, Mulungu anasonyezadi kuti ali ndi mphamvu youkitsa munthu wakufa. w17.12 4-5 ¶7-8

Loweruka, August 10

Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.​—Miy. 22:15.

Nzeru ndi zosiyana kwambiri ndi uchitsiru. Choncho tinganene kuti munthu akamachita zinthu mwanzeru umakhala umboni wakuti ndi wamkulu. Ndipo kukula mwauzimu sikudalira msinkhu wa munthu koma zimene amachita pomvera Yehova ndi mtima wonse komanso kumuopa.(Salimo 111:10) Achinyamata amene akula mwauzimu salola kuti zimene amalakalaka kapena zimene anzawo amachita ziwasokoneze. Tingati sakhala ‘otengekatengeka ngati kuti akukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku.’ (Aef. 4:14) M’malomwake ‘amaphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kuti azisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheb. 5:14) Iwo amasonyeza kuti akukula mwauzimu akamasankha zochita mwanzeru. Nzeru zoterezi n’zimene zingathandize munthu kuti adzapulumuke. (Miy. 24:14) Choncho muyenera kufotokozera ana anu momveka bwino mfundo za m’Baibulo zimene mumatsatira. Zolankhula komanso zochita zanu zizisonyeza kuti mumatsatiradi mfundo za m’Mawu a Mulungu.​—Aroma 2:21-23. w17.12 20-21 ¶12-13

Lamlungu, August 11

Pitirizani kuyenda mwanzeru pochita zinthu ndi anthu akunja . . . Mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.​—Akol. 4:5, 6.

Anthu ambiri angakopeke ndi maganizo oti anthu akhoza kuthetsa mavuto a m’dzikoli. Zili choncho chifukwa chakuti ngati maganizowa atakhala oona, ndiye kuti anthu sangafunike kutsogoleredwa ndi Mulungu komanso akhoza kumangochita zimene akufuna. Anthu ena amakhulupirira maganizo amenewa chifukwa chakuti ochita kafukufuku ena anapeza kuti nkhondo, uchigawenga, matenda komanso umphawi zikuchepa masiku ano. Lipoti lina linanena kuti: “Anthu ambiri ayamba kukhala ndi makhalidwe abwino chifukwa akufuna kuti zinthu ziziyenda bwino m’dzikoli.” Ngati mwamva maganizo a m’dziko amene akhoza kukusokonezani, muyenera kufufuza zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhaniyo komanso kukambirana ndi Mkhristu wina amene amadziwa zambiri. Ganizirani chifukwa chake mukhoza kukopeka ndi maganizowo, chifukwa chake ndi olakwika komanso zimene munganene pokambirana ndi munthu amene ali ndi maganizowo. Tonsefe tikhoza kupewa kutengera maganizo a m’dzikoli tikamatsatira malangizo amene Paulo anapereka mulemba la lero. w17.11 24 ¶14, 17

Lolemba, August 12

Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi.—Luka 18:11.

Kodi n’chifukwa chiyani Afarisi sankasonyeza ena chifundo? Baibulo limanena kuti iwo ankaona anthu “ena onse ngati opanda pake.” (Luka 18:9-14) Ifeyo tiyenera kutsanzira Yehova osati Afarisi. Tiyenera kusonyeza chifundo. (Akol. 3:13) Kuti tichite zimenezi, tiyenera kusonyeza kuti ndife okonzeka kukhululukira ena. (Luka 17:3, 4) Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimafulumira kukhululukira anthu amene andilakwira ngakhale mobwerezabwereza? Kodi ndimafunitsitsa kukhazikitsa mtendere ndi munthu amene wandilakwira kapena kundikhumudwitsa?’ Tikamakhululukira ena timasonyezanso kuti ndife odzichepetsa. Afarisi ankalephera kuchita zimenezi chifukwa chakuti ankadziona kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena. Koma Akhristufe tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumaona kuti anthu ‘ena ndi otiposa’ komanso oyenera kuwakhululukira. (Afil. 2:3) Kodi inuyo mudzayesetsa kukhala odzichepetsa n’kumatsanzira Yehova? Tinganene kuti tiyenera kukonza mtima wathu kuti tisamavutike kukhululukira anthu komanso anthu asamavutike kupempha kuti tiwakhululukire. Tizikhala ofulumira kuchitira ena chifundo, osati ofulumira kukhumudwa.​—Mlal. 7:8, 9. w17.11 14-15 ¶6-8

Lachiwiri, August 13

Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.—Sal. 147:1.

Mwina mumachita manyazi mukayerekezera mawu anu ndi mawu a anthu ena. Koma zimenezi siziyenera kukulepheretsani kukwaniritsa udindo wanu wotamanda Yehova pomuimbira nyimbo. Chongofunika ndi kutenga nyimbo yanu n’kuikweza m’mwamba, kudzutsa bwino mutu wanu, n’kumaimba kuchokera pansi pa mtima. (Ezara 3:11) Masiku ano, m’Nyumba za Ufumu zina mumakhala masikirini osonyeza mawu a nyimbo ndipo izi zimathandiza kuti anthu azikweza bwino mitu yawo poimba. N’zosangalatsanso kuti masiku ano pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu imene akulu amakhala nayo, pamakhalanso nthawi yoimba nyimbo. Zimenezi zikusonyeza kuti akulu ayenera kutsogolera mpingo pa nkhani yoimba. Anthu ena saimba mokweza chifukwa cha mantha. Amaopa kuti anthu ena sangasangalale ndi mawu awo. Tizikumbukira kuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri” tikamalankhula. (Yak. 3:2) Koma palibe amene amasiya kulankhulako. Choncho si bwino kusiya kutamanda Yehova chifukwa choganiza kuti mawu athu samveka bwino. w17.11 4-5 ¶9-10

Lachitatu, August 14

Mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.​—Zek. 6:15.

Zekariya ataona masomphenya ake a nambala 7, anali ndi zambiri zoti aganizire. Yehova analonjeza kuti adzalanga anthu amene amachita zinthu mwachinyengo. Lonjezoli liyenera kuti linalimbikitsa Zekariya. Koma pa nthawiyo anthu ankachitabe zachinyengo ndiponso zinthu zina zoipa. Komanso ntchito yomanga kachisi wa Yehova ku Yerusalemu inali isanapite patali. Kodi n’chiyani chinachititsa Ayuda kuti asiye kugwira ntchito imene Mulungu anawapatsayi? Kodi iwo anabwerera kwawo n’cholinga choti azikangochita zofuna zawo? Yehova ankadziwa zimene zingathandize anthu ake. Iye anaonetsa Zekariya masomphenya omaliza n’cholinga choti atsimikizire Ayuda kuti amawakonda ndipo amayamikira zonse zimene anachita pogwira ntchito yake. Yehova analonjeza Ayudawo mawu amulemba la lero powatsimikizira kuti adzakwanitsa kumanganso kachisi. w17.10 26 ¶1; 27 ¶5

Lachinayi, August 15

Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.​—Afil. 2:13.

Abale amene amalimba mtima n’kumayesetsa kuti akhale atumiki othandiza kapena akulu, amathandiza kwambiri mpingo. (1 Tim. 3:1) Koma abale ena safuna kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, m’bale amene anachita zinthu zolakwika m’mbuyomu akhoza kuganiza kuti si woyenerera kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu. Pomwe m’bale wina angaone kuti udindowu ndi waukulu kwambiri moti sangaukwanitse. Koma ngati muli ndi maganizo amenewa, Yehova angakuthandizeni kukhala olimba mtima. (Afil. 4:13) Kumbukirani kuti Mose nayenso ankaona kuti sangakwanitse ntchito imene Yehova anamupatsa. (Eks. 3:11) Koma Yehova anamuthandiza ndipo Mose analimba mtima n’kugwira bwinobwino ntchitoyo. Kuti m’bale wobatizidwa akhale wolimba mtima ayenera kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kumapempha Mulungu kuti amuthandize. Kuganizira nkhani za anthu amene anasonyeza kulimba mtima kungamuthandizenso. Akhozanso kupempha akulu kuti azimuphunzitsa ntchito zosiyanasiyana mumpingo ndipo ayenera kukhala wokonzeka kuchita chilichonse chimene angamupemphe. Tikulimbikitsa abale obatizidwa onse kuti akhale olimba mtima n’kumagwira ntchito mwakhama kuti azithandiza mumpingo. w17.09 32 ¶19

Lachisanu, August 16

Mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.​—Yes. 40:8.

Akhristu sayenera kuona kuti ntchito yomasulira Baibulo la Septuagint, la Wycliffe komanso la King James Version inkatsogoleredwa ndi mzimu woyera ngati mmene zinalili ndi Baibulo loyambirira. Komabe tikaganizira za Mabaibulo amenewa komanso Mabaibulo ena ambiri amene afalitsidwa, timaona umboni wakuti Mawu a Yehova adzakhalapobe mpaka kalekale ngati mmene iye analonjezera. Zimenezi zimatitsimikizira kuti malonjezo ena onse a Yehova adzakwaniritsidwa. (Yos. 23:14) Tikamaganizira kuti Baibulo likupezekabe masiku ano, timalimbikitsidwanso kukonda kwambiri Yehova. Koma kodi n’chifukwa chiyani Yehova anatipatsa Mawu ake? Nanga n’chifukwa chiyani anatitsimikizira kuti Mawu ake adzakhalapobe mpaka kalekale? Iye anachita zonsezi chifukwa chakuti amatikonda ndipo amafuna kutiphunzitsa kuti zinthu zizitiyendera bwino. (Yes. 48:17, 18) Popeza Yehova wasonyeza kuti amatikonda, ifenso tiyenera kumukonda ndiponso kumvera malamulo ake.​—1 Yoh. 4:19; 5:3. w17.09 21-22 ¶13-14

Loweruka, August 17

Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.​—Aef. 6:2.

Ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wosakhulupirira, kuphunzitsa ana kuti atsatire lamuloli kumakhala kovuta. Koma inuyo muyenera kumamulemekeza kuti mupereke chitsanzo chabwino kwa ana. Muyenera kuganizira kwambiri zinthu zimene amachita bwino ndipo muzimuyamikira. Pakakhala ana anu, muzipewa kulankhula zimene mwamuna kapena mkazi wanu amalakwitsa. Muzifotokozera anawo kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha kutumikira Yehova kapena ayi. Khalidwe labwino la ana anu likhoza kukopa mwamuna kapena mkazi wanuyo kuti nayenso ayambe kutumikira Mulungu. Amuna ena osakhulupirira amaletsa akazi awo kuti asamaphunzitse ana awo Baibulo kapena kupita nawo kumisonkhano. Ngakhale zitakhala choncho, mkazi wachikhristu amayesetsa kupeza njira yophunzitsira anawo mfundo zoona za m’Baibulo. (Mac. 16:1; 2 Tim. 3:14, 15) Mkaziyo ayenera kugonjera zimene mwamuna wake wanena komabe mwayi ukapezeka ayenera kufotokozera anawo zimene iyeyo amakhulupirira. Zimenezi zingawathandize kuphunzira makhalidwe abwino komanso mfundo zokhudza Yehova.​—Mac. 4:19, 20. w17.10 14 ¶9-10

Lamlungu, August 18

Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.

Anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Choncho popeza Yehova ndi wachifundo, ngakhale anthu amene sadziwa Mulungu amatha kusonyeza khalidweli. (Gen. 1:27) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anasonyeza chifundo. Mwachitsanzo, muli nkhani ya mahule awiri amene ankakanganirana mwana. Koma Solomo atalamula kuti mwanayo adulidwe, mayi weniweni anachitira mwanayo chifundo. Iye sanafune kuti mwanayo aphedwe moti ankaona kuti bola angotengedwa ndi mnzakeyo. (1 Maf. 3:23-27) Chitsanzo china ndi cha mwana wa Farao yemwe anapulumutsa Mose ali mwana. Iye anadziwa kuti mwanayo ndi wachiheberi ndipo ayenera kuphedwa. Koma “anamumvera chisoni” ndipo anasankha zoti amulere ngati mwana wake.​—Eks. 2:5, 6. w17.09 8-9 ¶2-3

Lolemba, August 19

[Yehova] akuleza nanu mtima.—2 Pet. 3:9.

Atumiki onse a Yehova ayenera kukhala odzichepetsa ndipo akamachita zimenezi amadalitsidwa. (Miy. 22:4) Tikamakhala odzichepetsa timathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere komanso mgwirizano. Tikamayesetsa kukhala odzichepetsa Mulungu amatisonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu. Paja mtumwi Petulo ananena kuti: “Nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa, chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Pet. 5:5) Masiku ano, anthu ofatsa komanso oleza mtima amaonedwa kuti ndi opepera. Koma maganizo amenewa ndi olakwika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti makhalidwe awiriwa amachokera kwa Mulungu yemwe ndi wamphamvu kuposa aliyense m’chilengedwe chonse. Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kufatsa komanso kuleza mtima. Mwachitsanzo, taganizirani zimene anachita kudzera mwa angelo ake pamene Abulahamu komanso Loti ankamufunsa mafunso. (Gen. 18:22-33; 19:18-21) Komanso kwa zaka zoposa 1,500, Yehova ankalezera mtima Aisiraeli omwe ankavuta kwambiri.​—Ezek. 33:11. w17.08 25 ¶13-14

Lachiwiri, August 20

Mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.​—Afil. 4:7.

Tizipemphera kuti tilandire mtendere wa Mulungu. Koma Paulo ananena kuti mtendere wa Mulungu “umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? Anthu ena anamasulira mawuwa kuti “umaposa chilichonse chimene tikulakalaka” kapena “umaposa mapulani onse amene anthu angakhale nawo.” Apa Paulo ankatanthauza kuti “mtendere wa Mulungu” umakhala wabwino kwambiri kuposa zimene tingaganizire. Choncho ngakhale titaona kuti palibiretu njira yothetsera vuto linalake, Yehova amadziwa njira yake ndipo angachite zimene sitikuyembekezera. (2 Pet. 2:9) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe ndi “mtendere wa Mulungu” tikamakumana ndi mavuto? Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu wathu Yehova n’kumene kungatithandize. Koma zimenezi zingatheke kudzera “mwa Khristu Yesu” yemwe anapereka moyo wake monga nsembe ya dipo. Kupereka nsembeyi ndi chinthu china chodabwitsa chimene Atate wathu anatichitira. Iye amagwiritsa ntchito dipoli kuti atikhululukire machimo athu ndipo timatha kukhala ndi chikumbumtima chabwino komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.​—Yoh. 14:6; Yak. 4:8; 1 Pet. 3:21. w17.08 10 ¶7; 12 ¶15

Lachitatu, August 21

Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu, ndipo mlendo sangalowerere pamene mtimawo ukusangalala.​—Miy. 14:10.

Nthawi zina munthu amene waferedwa amangodziwa yekha mmene akumvera mumtima mwake ndipo sangafotokoze bwinobwino mmene akumvera. Nthawi zina munthu angafotokoze mmene akumvera koma ena sangamvetse bwinobwino zimene akunenazo. Kunena zoona, n’zovuta kudziwa mawu amene tinganene kwa munthu amene akumva chisoni kwambiri. Koma nthawi zambiri chomwe chimafunika ndi ‘kulira ndi anthu amene akulira.’ (Aroma 12:15) Ngati simungathe kunena mawu olimbikitsa pamasom’pamaso, mukhoza kungolemba khadi, imelo, meseji kapena kalata. Mukhoza kungolembapo lemba limodzi lolimbikitsa, khalidwe lina labwino limene womwalirayo anali nalo kapena zinthu zina zosangalatsa zimene munachitira limodzi. Kupemphera ndi Akhristu anzathu amene aferedwa kapena kuwapempherera kumathandizanso kwambiri. w17.07 14-16 ¶13-16

Lachinayi, August 22

Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.—Mat. 19:6.

Tiyerekeze kuti banja lanu silikuyenda bwino mmene munkaganizira. Mwina zafika poti silikukusangalatsani ngakhale pang’ono. Zimene zingakuthandizeni ndi kuganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. Iye ankadziyerekezera kuti ndi mwamuna wa Aisiraeliwo. (Yes. 54:5; 62:4) Aisiraeli, omwe anali ngati mkazi wa Mulungu, anali ovuta kwambiri. Koma Yehova sanafulumire kuwasiya. Mobwerezabwereza ankawachitira chifundo ndipo ankakumbukira pangano limene anapangana nawo. (Sal. 106:43-45) Izi zikusonyeza kuti Yehova ndi wachikondi komanso wokhulupirika. Mabanja amene amakonda Mulungu amayesetsa kumutsanzira. Choncho ngati banja lawo silikuyenda bwino, sangalithetse pa zifukwa zosagwirizana ndi Malemba. Iwo amadziwa kuti Yehova amafuna kuti asasiyane. Malemba amasonyeza kuti munthu angathetse banja n’kukhala ndi ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso ngati mwamuna kapena mkazi wake wachita chigololo. (Mat. 19:5) Munthu akamachita zonse zimene angathe kuti banja lake liziyenda bwino amasonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova. w17.06 31 ¶17-18

Lachisanu, August 23

Maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu.—Gen. 3:5.

Zimene Satana anachita zachititsa kuti ulamuliro wa Yehova uzikayikiridwa. Iye amanena kuti ulamuliro wa Mulungu si wachilungamo. Amanenanso kuti Mulungu amamana anthu ndiponso angelo zinthu zabwino. Maganizo a Mdyerekezi ndi oti anthu akhoza kukhala osangalala ngati atamadzilamulira okha. (Gen. 3:1-4) Iye ananenanso kuti munthu aliyense sangakhale wokhulupirika kwa Yehova ndi mtima wonse, moti atayesedwa kwambiri akhoza kukana ulamuliro wake. (Yobu 2:4, 5) Choncho Yehova walola kuti anthu azidzilamulira n’cholinga choti anthuwo aone okha mavuto amene angakhalepo ngati sakulamuliridwa ndi Yehova, yemwe ndi wachilungamo. Popeza kuti Yehova amadziwa zoti zimene Satana amanenazi ndi zabodza, n’chifukwa chiyani walola kuti nkhaniyi itenge nthawi yaitali asanaithetse? Iye akudziwa kuti nkhaniyi ikukhudza anthu onse komanso angelo choncho m’pofunika kuti aliyense atsimikizire ngati zonena za Satanazo ndi zoona kapena ayi. (Sal. 83:18) Tisaiwalenso kuti anthu awiri oyambirira anakana ulamuliro wa Yehova ndipo izi n’zimene anthu ambiri akhala akuchita. Zimenezi zingachititse anthu ena kuganiza kuti zonena za Satanazi ndi zoona. w17.06 23 ¶3-4

Loweruka, August 24

Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga.​—Mat. 28:19.

Ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imatithandiza kuti tikhale akhama, tisamadzikayikire komanso tizitha kulankhula bwinobwino ndi anthu popanda kuwakhumudwitsa. (Miy. 21:5; 2 Tim. 2:24) Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti ntchitoyi imatithandizanso kudziwa bwino Malemba amene amatsimikizira kuti mfundo zimene timakhulupirira ndi zoona. Timaphunziranso kugwira ntchito limodzi ndi Yehova. (Akor. 3:9) Ntchito yolalikira imasangalatsabe ngakhale m’gawo limene anthu ambiri sakonda kumvetsera. Paja ntchitoyi ndi ya mpingo wonse osati munthu aliyense payekha. Ngakhale kuti m’bale kapena mlongo mmodzi ndi amene amapeza munthu yemwe amayamba kusonkhana, zoona zake n’zakuti mpingo wonse unkafufuza, choncho aliyense amasangalala. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Brandon amene analalikira m’gawo lovuta kwa zaka 9. Iye anati: “Chifikireni kugawoli sindinakhalepo ndi mwayi wothandiza munthu kufika pobatizidwa koma ena akwanitsa kuchita zimenezi. Ndimasangalala kwambiri kuti ndinasankhiratu kuti ndizichita zambiri pa ntchito yolalikira.”​—Mlal. 11:6. w17.07 23 ¶7; 24 ¶9-10

Lamlungu, August 25

Sanakhalenso ndi nkhawa.—1 Sam. 1:18.

Hana analibe mwana, pomwe mkazi wina wa Elikana dzina lake Penina anali ndi ana. (1 Sam. 1:4-7) “Chaka ndi chaka,” Penina ankanyoza Hana. Izi zinachititsa kuti Hana azidandaula kwambiri. Choncho anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize ndipo Baibulo limanena kuti anapemphera “kwa nthawi yaitali.” Ayenera kuti ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova ayankha pemphero lakeli chifukwa “sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:12) Iye ankaona kuti Yehova adzamuthandiza kuti akhale ndi mwana kapena kumulimbikitsa m’njira inayake. Popeza si ife angwiro komanso tili m’dziko la Satanali, tizikumanabe ndi mavuto. (1 Yoh. 5:19) Koma chosangalatsa n’chakuti tikhoza kupemphera kwa Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akor. 1:3) Paja Hana atavutika anapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima. Nafenso tikakumana ndi mavuto, tisamangotchula mmene tikumvera chifukwa cha mavutowo. Koma tizipemphera kuchokera mumtima n’kumachonderera Yehova kuti atithandize.​—Afil. 4:6, 7. w17.06 6 ¶10-11

Lolemba, August 26

Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?—Yoh. 21:15.

Yesu anadziwa kuti ophunzira ake sanaphe nsomba ngakhale imodzi ndipo anawauza kuti: “Ponyani ukonde kumbali ya kudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.” Ophunzirawo “anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukoka chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.” (Yoh. 21:1-6) Yesu anawakonzera chakudya cham’mawa, kenako anayang’ana Simoni Petulo n’kumufunsa funso lamulemba lalero. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pofunsa funso limeneli? Petulo ankakonda usodzi. Ndiye zikuoneka kuti Yesu ankafuna kudziwa ngati iye amakonda kwambiri ntchito ya usodzi kuposa mmene amakondera Yesu ndi mfundo zimene ankaphunzitsa. Petulo anayankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” (Yoh. 21:15) Zimene Petulo ankachita kuyambira tsiku limenelo zinasonyeza kuti ankakondadi Yesu. Iye ankalalikira mwakhama ndipo anali munthu wodalirika kwambiri mumpingo. w17.05 22 ¶1-2

Lachiwiri, August 27

Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?​—Aheb. 13:6.

Paulo ankatha kulimbana ndi mavuto ake chifukwa ankadziwa kuti Yehova amamukonda komanso kumuthandiza. Sankalola kuti mavuto amukhumudwitse kapena kumutayitsa mtima. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Nthawi zonse ankadalira “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Popanda kulankhula ndi Mulungu m’pemphero sitingakhale naye pa ubwenzi wabwino. (Sal. 86:3; 1 Ates. 5:17; Aroma 12:12) Tikamafotokozera Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” zimene zili mumtima mwathu komanso mmene tikumvera, timayamba kumukonda kwambiri. (Sal. 65:2) Ndiyeno tikaona kuti Yehova akuyankha mapemphero athu, chikondicho chimakula. Timafikanso pozindikira kuti “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.” (Sal. 145:18) Munthu akadziwa kuti Yehova amamuthandiza amatha kupirira mayesero aakulu kwambiri. w17.05 19 ¶9-10

Lachitatu, August 28

Yehova amaona mmene mtima ulili.​—1 Sam. 16:7.

Kodi inuyo mumatani ngati simukumvetsa kapena simukugwirizana ndi zimene akulu asankha? Kupanda kusamala zinthu ngati zimenezi zingalepheretse munthu kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Ndiye kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji? Taganizirani njira ziwiri zotsatirazi. Choyamba, kudzichepetsa kungatithandize kuvomereza kuti pakachitika nkhani sitingadziwe zonse. Kaya pangakhale zina zimene tikudziwa, koma tisaiwale kuti Yehova yekha ndi amene amaona mmene mtima ulili. Kudziwa mfundo imeneyi kungachititse kuti tiziona zinthu moyenera. Chachiwiri, kudzichepetsa kungatithandizenso kuti tizikhala ogonjera komanso oleza mtima n’kumadikira kuti Yehova akonze zinthu. Baibulo limati: “Woipayo sizidzamuyendera bwino n’komwe, ndiponso sadzachulukitsa masiku ake.” (Mlal. 8:12, 13) Tikakhala odzichepetsa zimatithandiza ifeyo komanso aliyense amene akukhudzidwa ndi nkhaniyo.​—1 Pet. 5:5. w17.04 25-26 ¶10-11

Lachinayi, August 29

Kuti ndipezeke kuno anachita chondiba kudziko la Aheberi, ndiponso kuno palibe chilichonse chimene ndinalakwa choti andiikire m’ndende muno.​—Gen. 40:15.

Zikuonekeratu kuti Yosefe sanachitiridwe chilungamo. Iye anafotokozanso kuti sanali wolakwa pa mlandu umene anamumangira. Choncho anapempha woperekera chikhoyo kuti akafotokozere Farao zimenezi. Iye ankafuna kuti munthuyo amuthandize kuti atuluke m’ndendemo. (Gen. 40:14) Yosefe sanangokhala osachita kalikonse pa mavuto ake. Iye ankadziwa kuti anthu akhala akumuchitira zinthu zopanda chilungamo. Choncho anafotokozera munthuyo zimene zinachitika n’cholinga choti amuthandize. Koma chochititsa chidwi n’chakuti Yosefe sanauze aliyense kuti abale ake ndi amene anamugulitsa. Iye sanauzenso Farao za nkhaniyi moti abale akewo atafika ku Iguputo n’kugwirizananso naye, Farao anawalandira bwino n’kuwauza kuti: “Zabwino za dziko lonse la Iguputo ndi zanu.”​—Gen. 45:16-20. w17.04 20-21 ¶12-13

Lachisanu, August 30

Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?—Aroma 11:33.

Chinthu china chochititsa kuti Yehova akhale woyenera kulamulira n’chakuti amadziwa chilichonse ndipo ali ndi nzeru zomuthandiza kusamalira chilengedwe chonse. Mwachitsanzo, iye anathandiza Mwana wake kuti achiritse matenda amene madokotala sakanachiza. (Mat. 4:23, 24; Maliko 5:25-29) Kwa Yehova zimenezi si zodabwitsa ayi. Iye amadziwa bwino matupi athu ndiponso zimene angachite kuti akonze chilichonse chimene chawonongeka. Akhozanso kuukitsa akufa kapena kuchititsa kuti ngozi zadzidzidzi zisamachitike padzikoli. Anthu a m’dziko la Satanali akukanika kuthetsa mikangano ya pakati pa mitundu ya anthu ndi mayiko. Koma Yehova yekha ndi amene ali ndi nzeru zothandiza kuti padziko lonse pakhale mtendere. (Yes. 2:3, 4; 54:13) Tikaphunzira bwinobwino nzeru za Yehova, timamva mmene anamvera mtumwi Paulo yemwe analemba mawu amulemba lathu la lero. w17.06 28 ¶6-7

Loweruka, August 31

Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.—Maliko 10:9.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri m’dzikoli ali ndi maganizo olakwika pa nkhani ya banja. Amaona kuti ngati pali vuto linalake ndi bwino kungomusiya mnzawoyo. Koma Akhristu amapewa maganizo amenewa. (1 Akor. 7:27) Munthu amene amaphwanya lonjezo lake pa nkhani ya ukwati amakhala kuti wanamiza Mulungu ndipo Mulungu amadana ndi anthu abodza. (Lev. 19:12; Miy. 6:16-19) Yehova amadana ndi anthu amene amathetsa banja popanda zifukwa za m’Malemba. (Mal. 2:13-16) Yesu ananena kuti banja likhoza kutha ngati wina wachita chigololo ndipo mnzakeyo wasankha kuti banjalo lithe. (Mat. 19:9; Aheb. 13:4) Nanga bwanji za kupatukana? M’Baibulo mulinso malangizo omveka bwino okhudza nkhani imeneyi. (1 Akor. 7:10, 11) Baibulo silitchula chifukwa chimene chingapangitse kuti anthu apatukane. Komabe Akhristu ena amaona kuti akhoza kupatukana ngati akukumana ndi mavuto aakulu omwe akuika moyo wawo pa ngozi kapena akuwalepheretsa kulambira Mulungu. Izi zingachitike ngati mnzawoyo amawachitira nkhanza kwambiri kapena ngati ndi wampatuko. w17.04 7-8 ¶14-16

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena