-
Zam’katimuMoyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
-
-
Zam’katimu
Tsamba
3 1. Moyo Wokhutiritsa—Kodi Ndi Wongoyerekeza Chabe?
5 2. Malangizo a Mmene Mungakhalire ndi Moyo Wokhutiritsa
11 3. Buku Lopereka Chithandizo Chodalirika
15 4. Wolemba Wamkulu wa Buku Lapaderalo
18 5. Mmene Mungam’dziŵire Mulungu
20 6. Kodi Yehova Anatilengeranji?
22 7. Moyo Wokhutiritsa—N’chifukwa Chiyani Uli Wosoŵa Choncho?
25 8. Njira Yobwerera ku Moyo Wokhutiritsa
28 9. Sangalalani ndi Moyo Wokhutiritsa—Tsopanolino ndi Kwamuyaya!
-
-
Moyo Wokhutiritsa—Mmene MungaupezereMoyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
-
-
Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
Taganizirani zodabwitsa izi: M’dziko lina lotukuka, anthu oposa 90 peresenti amaona kuti ali ndi moyo wachimwemwe kwambiri kapena wachimwemwe chokwanira ndithu. Koma mitundu ya mankhwala itatu pa mitundu khumi yogwiritsidwa ntchito kwambiri m’dzikomo imaperekedwa kaamba ka vuto la kuvutika maganizo. M’dziko lokhalokhalo, 91 peresenti ya anthu amaona kuti moyo wa banja lawo uli wokhutiritsa. Chikhalirechobe, pafupifupi theka la maukwati kumeneko amatha!
Ndipo kufufuza anthu m’mayiko 18, okwana pafupifupi theka la chiŵerengero cha anthu onse padziko lapansi, kumaonetsa kuti “anthu ambiri padziko lapansi akuopa za m’tsogolo.” Choncho, n’chachidziŵikire kuti ambiri sali ndi moyo wokhutiritsa. Nanga inuyo bwanji? Kabukuka kalembedwa kuti kakuthandizeni kupanga moyo wanu kukhala wokhutiritsa kwenikweni.
-