Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • la mutu 8 tsamba 25-27
  • Njira Yobwerera ku Moyo Wokhutiritsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Yobwerera ku Moyo Wokhutiritsa
  • Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Nthaŵi Imene Ukapolo Udzathe!
    Galamukani!—2002
  • Pamene Sikudzakhalanso Uchimo
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
la mutu 8 tsamba 25-27

Mutu 8

Njira Yobwerera ku Moyo Wokhutiritsa

1. Kodi Yehova anangowasiya anthu opanda chiyembekezo?

NGAKHALE kuti mtundu wa anthu onse unagwera m’njira ya moyo wopanda pake chifukwa chopandukira ulamuliro waumulungu, Mulungu sanangowasiya anthu opanda chiyembekezo. Baibulo limafotokoza kuti: “Cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:20, 21) Inde, Mulungu anapereka chiyembekezo kwa ana a banja loyambalo. Chinali chiyembekezo chotsimikizirika chonena kuti mtundu wa anthu onse ukamasulidwa ku uchimo wobadwa nawo ndi imfa. Iwo akayanjanitsidwanso paubale wachikondi ndi Yehova Mulungu. Motani?

2. Kodi zimene Adamu anachitira ana ake tingazifanizire ndi chiyani?

2 Pamene Adamu ndi Hava anachimwa, anatayira ana awo chiyembekezo chokhala ndi moyo wokhutiritsa padziko lapansi kosatha. Pofuna ufulu wosankha okha zabwino ndi zoipa, iwo anagulitsa banja lawo lam’tsogolo mu ukapolo ku uchimo ndi imfa. Pobadwira m’banja lotero, ana awo angafanizidwe ndi akapolo osungidwa pachilumba chakutali cholamulidwa ndi mafumu ankhanza. Inde, imfa yakhala ikulamulira monga mfumu pa anthu amene ali kale muukapolo kwa mfumu ina—uchimo. (Aroma 5:14, 21) Zikuoneka ngati palibe aliyense angawapulumutse akapolowo. Eya, kholo lawo lenilenilo n’limene linawagulitsa muukapolo umenewo! Koma munthu wina wachisomo akutumiza mwana wake, yemwe akufika ndi malipiro okwanira owombolera onse omangidwawo.—Salmo 51:5; 146:4; Aroma 8:2.

3. N’chifukwa chiyani Yesu Kristu anabadwa kwa namwali?

3 M’fanizo limeneli munthu amene akupulumutsa akapolo akuimira Yehova Mulungu. Mwana yemwe akufika ndi malipiro owawombolera ndiye Yesu Kristu. Asanadzakhale munthu iye anali ndi moyo wauzimu monga Mwana wa Mulungu wobadwa yekha. (Yohane 3:16) Iye anali cholengedwa choyambirira chenicheni cha Yehova, ndipo zolengedwa zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iyeyo. (Akolose 1:15, 16) Mwa chozizwitsa, Yehova anasamutsira moyo wa Mwana wake wauzimu m’mimba mwa namwali kotero kuti khandalo likabadwe monga munthu wangwiro yemwe akakhala ndi mtengo wokwaniritsa zofunika za chilungamo cha Mulungu.—Luka 1:26-31, 34, 35.

4. Kodi zina mwa ziphunzitso za Yesu Kristu n’zotani, ndipo n’chifukwa chiyani zili zogwira mtima?

4 Pamene Yesu anali ndi zaka ngati 30, anabatizidwa m’mtsinje wa Yordano. Pa ubatizo wake, anadzozedwa ndi mzimu woyera, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Zitatero, iye anakhala Kristu, kutanthauza “Wodzozedwa.” (Luka 3:21, 22) Utumiki wa Yesu padziko lapansi unatha zaka zitatu ndi theka. M’zaka zimenezo, anaphunzitsa atsatiri ake za “Ufumu wa Mulungu,” limene ndi boma lakumwamba limene lidzayanjanitsanso anthu onse paubale wamtendere ndi Yehova Mulungu. (Luka 4:43; Mateyu 4:17) Yesu ankadziŵa njira imene anthu angakhalire ndi moyo wa chisangalalo, ndipo anapatsa atsatiri ake malangizo achindunji a mmene angapezere chisangalalocho. Bwanji osatsegula Baibulo lanu pa Mateyu chaputala 5 mpaka 7 ndi kuŵerenga zina mwa ziphunzitso zake za Ulaliki wa pa Phiri?

5, 6. Kodi inuyo panokha mumamva bwanji poona zimene Yehova ndi Yesu achitira anthu?

5 Mosiyana ndi Adamu, Yesu anakhala ndi moyo womvera Mulungu m’njira iliyonse. Iye “sanachita tchimo.” (1 Petro 2:22; Ahebri 7:26) Ndipo iye anali ndi ufulu wokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi, koma ‘anataya moyo wake’ kuti alipire kwa Mulungu chimene Adamu anataya. Yesu anapereka moyo wake wangwiro waumunthu pamtengo wozunzikira. (Yohane 10:17; 19:17, 18, 28-30; Aroma 5:19, 21; Afilipi 2:8) Mwakutero, Yesu anapereka dipo, kapena kuti anapereka malipiro ofunikira kuwombola mtundu wa anthu onse ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Mateyu 20:28) Tayerekezani kuti mukugwira ntchito yoŵaŵa, ya malipiro ochepa kwambiri, komanso m’shopu kapena fakitale yauve, moti moyo ndi waukapolo weniweni. Kodi simungayamikire kwambiri munthu amene angakonze kuti akumasuleni mu ukapolo woterowo ndi amene angapereke moyo wake m’malo mwa inu? Kupyolera m’makonzedwe a dipo, njira inatseguka yakuti mubwerere ku banja la Mulungu la m’chilengedwe chonse ndi kukhala ndi moyo wokhutiritsa kwenikweni, wosakhalanso mu ukapolo ku uchimo ndi imfa.—2 Akorinto 5:14, 15.

6 Kudziŵa ndi kuyamikira chisomo cha Yehova chimenechi kumakupatsani chifukwa chokwanira choti mugwiritse ntchito m’moyo wanu mawu anzeru opezeka m’Baibulo. Mwachitsanzo, titenge limodzi la malangizo ovuta kwambiri kuwagwiritsa ntchito—kukhululukira ena pamene akulakwirani. Kodi mukukumbukira mawu opezeka pa Akolose chaputala 3, mavesi 12 mpaka 14, amene tinafotokoza mu Phunziro 2? Mavesi amenewo anakulimbikitsani kumakhululukira ena ngakhale pamene mungakhale ndi chifukwa chodandaulira za iwo. Nkhaniyo ikufotokoza chifukwa chake, mwa kunena kuti: “Monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” Mukalingalira mofatsa zimene Yehova ndi Yesu Kristu achitira anthu, mudzakakamizika kumakhululukira ena pa zolakwa zilizonse zimene angapange, makamaka ngati alapa ndi kupepesa.

[Mawu Otsindika patsamba 25]

Mulungu anapereka chiyembekezo kwa anthu kuti akamasuke mu ukapolo wa uchimo ndi imfa

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Kodi simungayamikire kwambiri munthu amene angakumasuleni mu ukapolo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena