January
Lachitatu, January 1
Moseyo anali munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.—Num. 12:3.
Mose ali m’banja lachifumu ku Iguputo, sanali wofatsa. Nthawi ina anapsa mtima kwambiri moti anapha munthu wina amene iye ankaona kuti sanachite zachilungamo. Mose ankaganiza kuti Yehova asangalala ndi zimene anachitazo. Choncho kwa zaka 40, Yehova anathandiza Mose kuzindikira kuti ankayenera kukhala wofatsa kuti atsogolere Aisiraeli osati kungokhala wolimba mtima basi. Komanso kuti akhale wofatsa, ankayenera kukhala wodzichepetsa, wogonjera ndiponso wodekha. Iye anaphunzira zimenezi ndipo anakhala mtsogoleri wabwino kwambiri. (Eks. 2:11, 12; Mac. 7:21-30, 36) Masiku ano, abale amene ali pa banja komanso akulu angachite bwino kutsanzira Mose. Sayenera kukwiya msanga ngati anthu ena sakuwalemekeza. Ayeneranso kuvomereza modzichepetsa zinthu zimene amalakwitsa. (Mlal. 7:9, 20) Ayenera kugonjera Yehova n’kumatsatira malangizo ake pothetsa mavuto. Komanso nthawi zonse ayenera kulankhula modekha. (Miy. 15:1) Abale a pa banja komanso akulu amene amachita zimenezi amasangalatsa Yehova, amalimbikitsa mtendere komanso amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kufatsa. w19.02 8 ¶1; 10 ¶9-10
Lachinayi, January 2
Anawamvera chifundo.—Maliko 6:34.
N’chifukwa chiyani Yesu anamvera chifundo anthu? Iye anaona kuti anthuwo “anali ngati nkhosa zopanda m’busa.” Mwina Yesu anazindikira kuti ena mwa anthuwo anali osauka ndipo ankagwira ntchito nthawi yaitali kuti apezere mabanja awo zinthu zofunika pa moyo. Mwina ena anali oferedwa. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Yesu ankamvetsa mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Yesu ayenera kuti anakumanapo ndi ena mwa mavuto amenewa. Iye ankaganizira anthu ena ndipo ankawachitira chifundo n’kumawauza uthenga wolimbikitsa. (Yes. 61:1, 2) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Nafenso timakumana ndi anthu amene ali ngati “nkhosa zopanda m’busa.” Anthuwo amakumana ndi mavuto ambirimbiri. Uthenga wa Ufumu, umene timalalikira, ndi umene ungawathandize kwambiri. (Chiv. 14:6) Choncho mofanana ndi Yesu, tiyenera kulalikira chifukwa ‘chomvera chisoni anthu onyozeka ndi osauka.’ (Sal. 72:13) Mtima wa chifundo umatilimbikitsa kuti tizithandiza anthu. w19.03 21-22 ¶6-7
Lachisanu, January 3
Adalitsike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.—Sal. 68:19.
Anthufe tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kukonda Yehova. Sikuti amangotipatsa zofunika pa moyo tsiku lililonse koma amatiphunzitsanso mfundo zoona zokhudza iyeyo komanso zolinga zake. (Yoh. 8:31, 32) Iye watipatsanso mpingo wachikhristu kuti uzititsogolera komanso kutithandiza. Amatithandizanso kuti tipirire mavuto athu panopa komanso watipatsa chiyembekezo choti tidzakhale ndi moyo wosatha tili angwiro. (Chiv. 21:3, 4) Tikaganizira zinthu zambiri zimene Yehova watichitira chifukwa cha chikondi timalimbikitsidwa kuti nafenso tizimukonda. Ndiyeno kukonda Yehova kumatithandiza kuti tizikhala ndi mantha oyenera n’kumaopa kumukhumudwitsa. Mukamazindikira ubwino wotsatira malangizo a Yehova m’pamene mumayambanso kumukonda kwambiri ndiponso kukonda mfundo zake. Zikatero, chilichonse chimene Satana angakunyengerereni nacho sichidzakupangitsani kuti musiye Yehova. Kodi mungamve bwanji mutakhala zaka zina 1000 kuchokera panopa? Mudzaona kuti munachita bwino kwambiri kudzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa. w19.03 6 ¶14; 7 ¶19
Loweruka, January 4
Mkazi wabwino, ndani angam’peze? Mtengo wake umaposa wa miyala yamtengo wapatali.—Miy. 31:10.
Anthu m’banja akamayamikirana zinthu zimayenda bwino. Mwamuna ndi mkazi wake akamayamikirana kwambiri banja lawo limalimbanso kwambiri ndipo savutika kukhululukirana. Mwamuna amene amayamikira mkazi wake amaona zinthu zabwino zimene iye amachita ndipo “amaimirira n’kumuuza kuti ndi wodala.” (Miy. 31:28) Nayenso mkazi wanzeru amayamikira zinthu zabwino zimene mwamuna wake amachita. Ngati ndinu makolo, kodi mungatani kuti muziphunzitsa ana anu kuti akhale oyamikira? Muzikumbukira kuti ana amatengera zimene inuyo mumachita ndiponso kulankhula. Choncho muzipereka chitsanzo chabwino ponena kuti zikomo ana anu akakuchitirani zinazake. Komanso muziphunzitsa ana anu kunena kuti zikomo anthu ena akawachitira zinthu zabwino. Muziwathandiza kudziwa kuti mawu oyamikira ayenera kuchokera mumtima komanso mawuwo akhoza kulimbikitsa kwambiri anthu. w19.02 17 ¶14-15
Lamlungu, January 5
Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.—Yobu 27:5.
Apatu Yobu anasonyeza kuti anali wotsimikiza mtima kuti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu ndipo ifenso tingachite chimodzimodzi. Satana amatsutsanso zoti aliyense wa ife angapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. Kodi zimenezi zimakukhudzani bwanji inuyo? Tingati Satana amanena kuti simukonda kwenikweni Yehova Mulungu, mudzasiya kumutumikira moyo wanu ukadzakhala pa ngozi komanso simungapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. (Yobu 2:4, 5; Chiv. 12:10) Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimenezi? Muyenera kuti mumakhumudwa. Koma taganizirani mfundo iyi: Yehova amakukhulupirirani kwambiri moti amalola kuti Satana akuyeseni. Iye amadziwa kuti mukhoza kukhalabe ndi mtima wosagawanika ndipo mudzasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Komanso Yehova walonjeza kuti adzakuthandizani kuchita zimenezi. (Aheb. 13:6) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kuti Yehova amatikhulupirira chonchi. Kukhala ndi mtima wosagawanika n’kofunika kwambiri. Zili choncho chifukwa timasonyeza kuti Satana ndi wabodza, timalemekeza dzina labwino la Atate wathu komanso timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. w19.02 5 ¶9-10
Lolemba, January 6
Nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.—Yoh. 16:2.
Yesu anauza atumwi ake mavuto amene iwo adzakumane nawo. Ndiyeno anawalimbikitsa kuti atengere chitsanzo chake powauza kuti, “Limbani mtima.” (Yoh. 16:1-4a, 33) Patapita zaka zambiri, ophunzira a Yesu ankamutsanzirabe pa nkhani yodzipereka komanso kulimba mtima. Iwo ankalolera kuvutika n’cholinga choti athandizane pa mavuto osiyanasiyana. (Aheb. 10:33, 34) Ifenso timatsanzira Yesu pa nkhani yolimba mtima. Mwachitsanzo, timalimba mtima kuti tithandize abale athu amene akuzunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Nthawi zina, abale athu amamangidwa popanda chifukwa. Zimenezi zikachitika tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize. (Afil. 1:14; Aheb. 13:19) Timasonyezanso kulimba mtima tikamapitiriza kulalikira mopanda mantha. (Mac. 14:3) Mofanana ndi Yesu, timalalikirabe uthenga wa Ufumu ngakhale pamene anthu akutitsutsa kapena kutizunza. w19.01 22-23 ¶8-9
Lachiwiri, January 7
Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane.—Aheb. 10:24, 25.
Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti muzipereka ndemanga zolimbikitsa kumisonkhano? Chofunika kwambiri ndi kukonzekera misonkhano yonse. Mukakonzekera bwino, mukhoza kulimba mtima kuti muyankhe. (Miy. 21:5) Kodi tingatani kuti tizikonzekera bwino? Musanayambe kukonzekera, muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu woyera. (Luka 11:13; 1 Yoh. 5:14) Kenako muziona mwachidule zimene zili munkhaniyo. Mwachitsanzo, muziona mutu, timitu ting’onoting’ono, zithunzi komanso mabokosi. Ndiyeno mukayamba kuphunzira ndime iliyonse, muziyesetsa kuwerenga malemba osagwidwa mawu. Muziganizira kwambiri nkhaniyo n’kuona mfundo zimene mungakayankhe. Mukakonzekera bwino, nkhaniyo imakufikani pamtima kwambiri ndipo zimakhala zosavuta kuti mukayankhe.—2 Akor. 9:6. w19.01 9 ¶6; 11-12 ¶13-15
Lachitatu, January 8
Lemba masomphenyawa.—Hab. 2:2.
Popeza Yehova analola Habakuku kuti alembe maganizo ake, kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikuphunzira kuti tisamaope kumufotokozera zimene zikutidetsa nkhawa kapena kutikayikitsa. Yehova amatilimbikitsa kuti tizipemphera kwa iye n’kumamukhuthulira zamumtima mwathu. (Sal. 50:15; 62:8) Habakuku ankayesetsa kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo ankamuona kuti ndi Mnzake wapamtima komanso Atate wake. Iye sankaona kuti alibiretu mtengo wogwira ndipo anapewa kudalira luso lake lomvetsa zinthu. M’malomwake anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopemphera n’kumafotokozera Yehova nkhawa zake. Ndipotu Yehova, yemwe ndi Wakumva pemphero, amatiuza kuti tizisonyeza kuti timamudalira popemphera kwa iye n’kumuuza zonse zimene zikutidetsa nkhawa. (Sal. 65:2) Tikamatero tidzaona Yehova akutithandiza ngati kuti watikumbatira n’kumatitsogolera mokoma mtima. (Sal. 73:23, 24) Iye adzatithandiza kuzindikira maganizo ake pa chilichonse chimene chikutisautsa mtima. Ndipotu munthu akamapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima m’pamene amasonyeza kuti amamudalira kwambiri. w18.11 13 ¶2; 14 ¶5-6
Lachinayi, January 9
Oyera amene ali padziko lapansi. Anthu aulemerero amenewo, ndi amene ndimakondwera nawo.—Sal. 16:3.
Davide sankacheza ndi anthu amsinkhu wake okha. Kodi mukukumbukira mmodzi mwa “anthu aulemerero” amene anali mnzake wapamtima? Anali Yonatani. Baibulo limasonyeza kuti awiriwa anali pa ubwenzi wabwino kwambiri. Komatu Yonatani anali wamkulu moti ankasiyana ndi Davide zaka 30. Ndiye kodi zinatheka bwanji kuti ayambe kugwirizana? Onse ankakhulupirira Mulungu, ankalemekezana komanso anali olimba mtima pomenyana ndi adani a Mulungu. (1 Sam. 13:3; 14:13; 17:48-50; 18:1) Ifenso tikhoza kukhala osangalala kwambiri tikamagwirizana ndi anthu amene amakonda Yehova komanso kumukhulupirira. Mlongo wina dzina lake Kiera, yemwe watumikira Mulungu kwa zaka zambiri, anati: “Ndili ndi anzanga a m’mayiko osiyanasiyana komanso azikhalidwe zosiyanasiyana.” Inunso mukamayesetsa kucheza ndi anthu osiyanasiyana mudzaona umboni wakuti Mawu a Mulungu komanso mzimu wake zimathandiza anthu kuti azigwirizana. w18.12 26 ¶11-13
Lachisanu, January 10
Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.—Mat. 19:9.
Mawu akuti dama amanena za zinthu monga chigololo, uhule, kugonana pakati pa anthu amene sali pa banja, kugonana amuna kapena akazi okhaokha komanso kugona nyama. Ngati mwamuna wachita dama, mkazi wake angasankhe kuthetsa banja kapena ayi. Akasankha kuthetsa banjalo ndiye kuti lathanso pamaso pa Mulungu. Koma Yesu sananene kuti munthu wina m’banja akachita dama ndiye kuti winayo amafunika kuthetsa banja basi. Mwachitsanzo, mkazi amene mwamuna wake wachita dama akhoza kusankha kuti akhalebe naye pa banja. Mwina amamukondabe ndipo akufuna kumukhululukira n’kumayesetsa kuti banja lawo liziyenda bwino. Komanso akathetsa banja n’kumakhala wosakwatiwa akhoza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, akhoza kuvutika kupeza zofunika pa moyo, angasowe wocheza naye komanso wogonana naye. (1 Akor. 7:14) Choncho n’zoonekeratu kuti mwamuna kapena mkazi wosalakwa akasankha kuthetsa banja akhoza kukumana ndi mavuto ena. w18.12 12 ¶10-11
Loweruka, January 11
Inu okonda Yehova danani nacho choipa.—Sal. 97:10.
Yehova amadana ndi zinthu zopanda chilungamo. (Yes. 61:8) Iye amadziwa kuti uchimo umene tinatengera umachititsa kuti nthawi zina tizikhala ndi maganizo olakwika. Koma amatiuza kuti nafenso tizidana ndi zinthu zopanda chilungamo. Kuganizira chifukwa chake Yehova amadana ndi zoipa kungatithandize kuti tikhale ndi maganizo ake pa nkhani imeneyi ndipo zingatilimbikitse kuti tizidana kwambiri ndi zoipazo. Munthu akakhala ndi maganizo a Yehova pa nkhani imeneyi, akhoza kudziwa kuti kuchita zinazake n’kulakwa ngakhale kuti zinthuzo sizinatchulidwe mwachindunji m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, masiku ano anthu akumakonda kavinidwe kena kofananako ndi kugonana. Ena amaganiza kuti kavinidwe kameneka si koipa ngati kugonana kwenikweni. Koma kodi zimenezi zimasonyeza kuti munthu ali ndi maganizo a Mulungu, amene amadana ndi zoipa zilizonse? Tiyeni tizipeweratu zoipa pokhala odziletsa ndipo tizidana kwambiri ndi zinthu zimene Yehova amadana nazo.—Aroma 12:9. w18.11 25 ¶11-12
Lamlungu, January 12
Wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.—Hab. 2:4.
Mtumwi Paulo anaona kuti limeneli ndi lonjezo la Yehova lofunika kwambiri moti anagwira mawu amenewa katatu. (Aroma 1:17; Agal. 3:11; Aheb. 10:38) Kaya wolungama akumane ndi mavuto otani, chikhulupiriro chake chingamuthandize kuti adzapeze moyo wosatha n’kudzaona cholinga cha Yehova chikukwaniritsidwa. Yehova amafuna kuti tiziona patali. M’buku la Habakuku muli phunziro lofunika kwambiri kwa anthu amene tikukhala m’masiku otsirizafe. Yehova akutitsimikizira kuti adzapereka moyo wosatha kwa wolungama aliyense amene amasonyeza kuti amamukhulupirira. Choncho kaya tikumane ndi mavuto otani, tiyeni tizilimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova. M’buku la Habakuku, Yehova watitsimikiziranso kuti adzatithandiza komanso kutipulumutsa. Iye amangotipempha kuti tizimukhulupirira komanso kuyembekezera moleza mtima Ufumu wake. Mu Ufumuwo, padziko lonse padzakhala atumiki ake ofatsa komanso osangalala okhaokha.—Mat. 5:5; Aheb. 10:36-39. w18.11 16-17 ¶15-17
Lolemba, January 13
[Pitirizani kuyenda] m’choonadi.—3 Yoh 4.
Mu nthawi ya Yesu, anthu ena amene poyamba anamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa sanapitirize kuyenda m’choonadi. Mwachitsanzo, chigulu cha anthu chitadyetsedwa mozizwitsa ndi Yesu, chinamutsatira kumbali ina ya nyanja ya Galileya. Ali kumeneko, Yesu ananena zinthu zimene zinawadabwitsa kwambiri. Iye anati: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, mulibe moyo mwa inu.” M’malo momupempha Yesu kuti awafotokozere zimene ankatanthauza, iwo anakhumudwa ndipo anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?” Pa chifukwa chimenechi, “ophunzira ake ambiri anamusiya ndi kubwerera ku zinthu zakumbuyo, ndipo sanayendenso naye.” (Yoh. 6:53-66) N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ena sapitirizanso kuyenda m’choonadi. Ena anakhumudwa chifukwa cha zimene m’bale waudindo ananena kapena kuchita. Ena anakhumudwa chifukwa cha malangizo ochokera m’Malemba omwe anapatsidwa kapena analolera kusiya choonadi chifukwa chosemphana maganizo ndi Mkhristu mnzawo. w18.11 9 ¶3-5
Lachiwiri, January 14
Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.—Mat. 23:10.
Ngati tikuvutika kumvetsa chifukwa chimene zinthu zina zasinthira m’gulu lathu, tingachite bwino kuganizira mmene Khristu ankachitira zinthu m’mbuyomu potsogolera anthu. Munthawi ya Yoswa komanso ya Akhristu oyambirira, Khristu ankapereka malangizo anzeru omwe ankateteza gulu la Mulungu, kulimbitsa chikhulupiriro cha anthu ake komanso kuwathandiza kuti azigwirizana. (Aheb. 13:8) Malangizo a pa nthawi yake amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka amasonyeza kuti Yesu amatifunira zabwino potumikira Mulungu. (Mat. 24:45) Tikamaona kuti Khristu akutitsogolera timazindikira kuti amafuna kuti tisabwerere m’mbuyo potumikira Mulungu. Kuwonjezera pa kutisamalira mwauzimu, Khristu amatithandiza kugwira mwakhama ntchito yofunika kwambiri padziko lonse, yomwe ndi yolalikira.—Maliko 13:10. w18.10 25 ¶13-16
Lachitatu, January 15
Muziyenda moyenera kuitana kumene munaitanidwa nako. Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse.—Aef. 4:1, 2.
Kudzichepetsa kumathandizanso kuti tikhale odziletsa ena akatiputa. (Aef. 4:2) Chitsanzo tingachipeze pa 2 Samueli 16:5-13. Davide ndi atumiki ake ananyozedwa komanso kugendedwa ndi Simeyi, yemwe anali wachibale wa Mfumu Sauli. Davide anali ndi mphamvu koma anadziletsa kuti asabwezere. Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti adziletse? Tingapeze yankho la funsoli mu Salimo 3. Mawu apamwamba pa Salimo 3 amasonyeza kuti salimoli ndi nyimbo ya Davide imene analemba pa nthawi imene “anali kuthawa mwana wake Abisalomu.” Vesi 1 ndi 2 limafotokoza zinthu zimene zili m’chaputala 16 cha buku la 2 Samueli. Lemba la Salimo 3:4 limasonyeza kuti Davide ankadalira kwambiri Yehova. Iye anati: “Ndidzafuulira Yehova mokweza, ndipo iye adzandiyankha.” Ifenso tiyenera kupemphera tikakhala pa mavuto. Tikatero Yehova amatipatsa mzimu woyera umene ungatithandize kuti tipirire. Kodi pali vuto lina limene mukukumana nalo ndipo mukufunika kudziletsa? Kapena kodi pali munthu winawake amene amadana nanu popanda chifukwa yemwe mukufunika kumukhululukira? Kodi mukukhulupirira kuti Yehova akuona mavuto anu ndipo angakudalitseni? w18.09 6-7 ¶16-17
Lachinayi, January 16
Ndife antchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.
Nthawi zonse tikamalalikira tiyenera kuchita zinthu mwaulemu komanso moganizira anthu. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kuwadziwa bwino anthu a m’gawo lathu. Tizikumbukira kuti tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, timapita kwa anthu omwe sanatiitane. Choncho ndi bwino kuwapeza pa nthawi imene angamasuke kukambirana nafe. (Mat. 7:12) Mwachitsanzo, kodi anthu m’gawo lanu amadzuka mochedwa Loweruka kapena Lamlungu? Ngati ndi choncho, ndi bwino kuyamba ndi kulalikira mumsewu kapena m’malo opezeka anthu ambiri. Apo ayi, tingapite kwa anthu amene tikudziwiratu kuti tikawapeza atadzuka. Anthu ambiri masiku ano amatanganidwa choncho si bwino kulankhula nawo kwa nthawi yaitali pa maulendo oyambirira. Ndi bwino kuwasiya msanga kusiyana ndi kuwachedwetsa. (1 Akor. 9:20-23) Anthu akaona kuti tikuzindikira zoti atanganidwa angalole mosavuta kuti tidzawapezenso ulendo wina. Tikakhala mu utumiki tiyenera kusonyeza makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. Tikamatero timakhaladi “antchito anzake a Mulungu” ndipo iye akhoza kutigwiritsa ntchito pokokera anthu ena m’gulu lake.—1 Akor. 3:6, 7. w18.09 32 ¶15-17
Lachisanu, January 17
Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.—Mat. 5:5.
Kodi kukhala wofatsa kungathandize bwanji kuti munthu akhale wosangalala? Munthu akaphunzira choonadi amasintha makhalidwe ake. Pali anthu ena amene anali ankhanza, okonda kukangana komanso aukali. Koma anavala umunthu watsopano ndipo amasonyeza “chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:9-12) Izi zimawathandiza kuti azikhala mwamtendere, azikondana ndi anthu komanso azikhala osangalala. Mawu a Mulungu amalonjeza kuti anthu oterewa “adzalandira dziko lapansi.” (Sal. 37:8-10, 29) Kodi mawu akuti ofatsa “adzalandira dziko lapansi” amatanthauza chiyani? Odzozedwa adzalandira dziko lapansi akadzayamba kulilamulira ngati mafumu ndi ansembe. (Chiv. 20:6) Koma anthu mamiliyoni ambiri amene sakupita kumwamba adzalandira dzikoli akadzaloledwa kukhalamo kwamuyaya. Pa nthawiyo adzakhala angwiro ndipo azidzakhala mwamtendere komanso mosangalala. w18.09 19 ¶8-9
Loweruka, January 18
Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.—Yak. 1:19.
Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. (Gen. 18:32; Yos. 10:14) Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya pa Ekisodo 32:11-14. Ngakhale kuti Yehova akanatha kuchita zinthu popanda kumva maganizo a Mose, anamupatsa mpata kuti afotokoze zimene ankaganiza. Anthu ambiri sangataye nthawi kumvetsera maganizo a munthu yemwe nthawi zina maganizo ake sakhala olondola ndipo sangatsatire zimene wanena. Koma Yehova amamvetsera moleza mtima anthu amene amapemphera kwa iye mwachikhulupiriro. Choncho aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Ngati Yehova anamvetsera anthu monga Abulahamu, Rakele, Mose, Yoswa, Manowa, Eliya, ndi Hezekiya, kuli bwanji ineyo? Kodi inenso ndimayesetsa kulemekeza abale ndi alongo n’kumawamvetsera akamalankhula ndiponso kutsatira maganizo awo omwe ndi othandiza? Nanga pali munthu wina mumpingo kapena m’banja langa amene akufunika kwambiri kuti ndizimumvetsera? Kodi ndiyenera kuchita chiyani?—Gen. 30:6; Ower. 13:9; 1 Maf. 17:22; 2 Mbiri 30:20. w18.09 6 ¶14-15
Lamlungu, January 19
Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto, ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.—Miy. 11:25.
Zingakhale zovuta kuti tikhalebe opatsa chifukwa tikukhala m’dziko limene anthu ambiri saganizira zofuna za anzawo. Koma Yesu ananena kuti lamulo lalikulu kwambiri ndi loti tizikonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse. Lachiwiri lake ndi loti tizikonda anzathu ngati mmene timadzikondera tokha. (Maliko 12:28-31) Anthu amene amakonda Yehova amamutsanzira. Yehova komanso Yesu ali ndi mtima wopatsa. Ndiye amatiuza kuti tizichitanso zomwezo chifukwa zingatithandize kukhala osangalala. Tiyeni tiziyesetsa kukhala opatsa kwa Mulungu komanso anzathu. Tikamatero, tidzalemekeza Yehova, kuthandiza anthu ena ndipo tidzakhala osangalala. Muyenera kuti mumayesetsa kuthandiza anthu, makamaka Akhristu anzanu. (Agal. 6:10) Mukamapitiriza kuchita zimenezi, anthu azikukondani komanso mudzakhala osangalala. w18.08 22 ¶19-20
Lolemba, January 20
Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja.—Yoh. 7:24.
Yehova saweruza anthu potengera mtundu, dziko, fuko kapena chilankhulo chawo. Iye amalandira munthu aliyense amene amamuopa komanso kuchita zimene amafuna. (Agal. 3:26-28; Chiv. 7:9, 10) N’zosachita kufunsa kuti nanunso mumakhulupirira mfundo imeneyi. Koma bwanji ngati munabadwira m’dziko kapena m’banja latsankho? Mwina mungamaganize kuti mulibe tsankho pomwe mumtima mwenimwenimo mudakali tsankho. Ngakhale Petulo, amene anagwiritsidwa ntchito pouza anthu kuti Mulungu alibe tsankho, pa nthawi ina anachita zinthu mwatsankho. (Agal. 2:11-14) Ndiye kodi tingapewe bwanji kuweruza anthu potengera maonekedwe awo? Tonsefe tiyenera kudzifufuza pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti tione ngati tidakali ndi kamtima katsankho. (Sal. 119:105) Tizivomerezanso ngati anzathu akutiuza kuti tili ndi kamtima kameneka ngakhale kuti ifeyo tikuganiza kuti tilibe. (Agal. 2:11, 14) N’zotheka kuti tsankholo linatilowerera kwambiri moti sitizindikira n’komwe kuti tili nalo. w18.08 9 ¶5-6
Lachiwiri, January 21
Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu.—Mat. 5:16.
Mungadzifunse kuti: ‘Kodi anthu onse amaona kuti ndine wodzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse? Kodi mpata ukapezeka ndimaugwiritsa ntchito kuti anthu adziwe zoti ndine wa Mboni za Yehova?’ Popeza Yehova anatisankha kuti tikhale m’gulu la anthu ake, angakhumudwe kwambiri ngati ataona kuti sitikufuna kudziwika kuti ndife Mboni zake. (Sal. 119:46; Maliko 8:38) N’zomvetsa chisoni kuti atumiki a Yehova ena amayamba kutengera “mzimu wa dziko” moti zochita zawo siziwasiyanitsa kwenikweni ndi anthu amene satumikira Mulungu. (1 Akor. 2:12) Mzimu wa dzikoli umalimbikitsa anthu kuti azichita “zofuna za thupi.” (Aef. 2:3) Mwachitsanzo, ngakhale kuti gulu lakhala likupereka malangizo pa nkhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa, anthu ena amachitabe zinthu motayirira. Amavala zovala zothina kapena zoonetsa mkati ngakhale kumisonkhano yathu. Apo ayi amameta kapena kupesa m’njira yachilendo kwambiri. (1 Tim. 2:9, 10) Chifukwa cha zimenezi, anthu oterewa akakhala ndi anthu ena munthu sangasiyanitse pakati pa atumiki a Yehova ndi ‘mabwenzi a dzikoli.’—Yak. 4:4. w18.07 24-25 ¶11-12
Lachitatu, January 22
Nonsenu ndinu abale.—Mat. 23:8.
Tinganene kuti tonsefe ndife “abale” chifukwa tonsefe ndi ana a Adamu. (Mac. 17:26) Koma pali chifukwa chinanso. Yesu ananena kuti ophunzira ake anali ngati abale ndi alongo chifukwa choti onse ankaona kuti Yehova ndi Atate wawo wakumwamba. (Mat. 12:50) Chinanso n’chakuti anakhala ngati banja limodzi lauzimu chifukwa choti chikondi ndi chikhulupiriro zinkawathandiza kukhala ogwirizana. N’chifukwa chake atumwi akamalemba makalata awo ankakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti ‘abale ndi alongo’ pofotokoza za Akhristu anzawo. (Aroma 1:13; 1 Pet. 2:17; 1 Yoh. 3:13) Yesu atasonyeza kuti tonsefe ndife abale ndi alongo, anatsindika kufunika kwa mtima wodzichepetsa. (Mat. 23:11, 12) Mtima wodzikuza ndi umene unachititsa kuti atumwi azikangana. Ndipo n’kutheka kuti mtima wonyadira mtundu wawo ndi umene unkawachititsanso zimenezi. Koma kodi zinalidi zomveka kuti Ayuda azinyada chifukwa choti anali ana a Abulahamu? Ayuda ambiri anali ndi maganizo amenewa. Koma Yohane M’batizi anawauza kuti: “Mulungu ali ndi mphamvu yokhoza kuutsira Abulahamu ana kuchokera ku miyala iyi.”—Luka 3:8. w18.06 9-10 ¶8-9
Lachinayi, January 23
Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu.—Miy. 17:27.
Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapewa kupsa mtima kapena kulankhula mawu oipa ndikapanikizika ndi mavuto kapena anthu ena akamandikhumudwitsa mobwerezabwereza?’ (Miy. 10:19; Mat. 5:22) Anthu ena akatiputa, tiyenera ‘kusiyira malo mkwiyo wa Yehova.’ (Aroma 12:17-21) Tikamadalirabe Yehova tidzasonyeza kuti timamulemekeza n’kupereka mpata woti asonyeze mkwiyo wake. Tingati timadekha n’kumayembekezera kuti iye akonze zinthu pa nthawi imene akuona kuti ndi yoyenera. Koma ngati tingafune kubwezera tokha zingatanthauze kuti sitilemekeza Yehova. Kodi timayesetsa kutsatira mokhulupirika malangizo atsopano amene Yehova watipatsa? Ngati timatero tidzapewa mtima wongofuna kuchita zinthu m’njira imene tinazolowera. M’malomwake tiziyesetsa kutsatira malangizo atsopano alionse amene Yehova angatipatse kudzera m’gulu lake. (Aheb. 13:17) Komanso tidzapewa ‘kupitirira zinthu zolembedwa.’ (1 Akor. 4:6) Tikamatero ndiye kuti tikuyang’anabe kwa Yehova. w18.07 15-16 ¶17-18
Lachisanu, January 24
Tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.—Aheb. 6:1.
Munthu akamakula mwauzimu amayamba kuona kuti mfundo za Mulungu ndi zofunika kwambiri. Zili choncho chifukwa malamulo angathandize pa nkhani imodzi koma mfundo zimathandiza pa nkhani zosiyanasiyana. Munthu akakhala wamng’ono sangamvetse kuopsa kocheza ndi anthu oipa, choncho makolo akhoza kumupatsa malamulo amene angamuteteze pa nkhaniyi. (1 Akor. 15:33) Koma akamakula, amayamba kumvetsa zinthu n’kumaganizira mfundo za m’Baibulo. Choncho amatha kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo. (1 Akor. 13:11; 14:20) Tikamaganizira mfundo za Mulungu chikumbumtima chathu chimatha kutitsogolera kuti tizisankha zinthu zimene Mulungu angasangalale nazo. Kodi tili ndi zonse zofunika kuti tizisankha zinthu mwanzeru n’kumasangalatsa Yehova? Inde. Tikamagwiritsa ntchito mwanzeru malamulo ndiponso mfundo za m’Mawu a Mulungu tidzakhala ‘oyenerera bwino komanso okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Tim. 3:16, 17. w18.06 19 ¶14; 20 ¶16-17
Loweruka, January 25
Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?—Luka 10:29.
Fanizo la Yesu linasonyeza kuti Msamariya akhoza kuthandiza Ayuda kuzindikira mmene angasonyezere chikondi chenicheni. (Luka 10:25-37) Ophunzira a Yesu ankafunika kuthetsa mtima wodzikuza komanso watsankho kuti agwire bwino ntchito imene anapatsidwa. Yesu asanapite kumwamba, anawauza kuti akhale mboni zake “ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Yesu anawakonzekeretsa kuchita zimenezi pamene anawathandiza kuzindikira makhalidwe abwino amene anthu amitundu ina anali nawo. Mwachitsanzo, iye anayamikira kapitawo wa asilikali chifukwa cha chikhulupiriro chake champhamvu. (Mat. 8:5-10) Ali kwawo ku Nazareti, Yesu anauza anthu zinthu zabwino zimene Mulungu anachitira anthu amitundu ina monga mkazi wamasiye wa ku Zarefati komanso Namani wa ku Siriya. (Luka 4:25-27) Ndipo Yesuyo analalikira mkazi wachisamariya kenako anakhalabe m’tauni ina ya Asamariya kwa masiku awiri chifukwa anthu ambiri ankafuna kumva uthenga wake.—Yoh. 4:21-24, 40. w18.06 10 ¶10-11
Lamlungu, January 26
Valani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu kuti musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.—Aef. 6:11.
Mtumwi Paulo anayerekezera moyo wa Akhristufe ndi zimene zimachitika ndi msilikali amene akumenyana ndi mdani pafupi. N’zoona kuti nkhondo imene tikumenya si yeniyeni koma yauzimu. Ngakhale zili choncho, adani athu ndi enieni. Satana ndi ziwanda zake ndi akatswiri pa nkhondo ndipo akhala akuimenya kwa zaka zambirimbiri. Kungoganizira zimenezi, munthu angaone kuti sangapambane. Makamaka achinyamata ndi amene amaoneka kuti akhoza kupezereredwa ndi adaniwa. Ndiye kodi angatani kuti apambane pa nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziwanda, omwe ndi amphamvu kwambiri? Chosangalatsa n’chakuti achinyamata akhoza kupambana pa nkhondoyi ndipo n’zimene zikuchitikadi. Zimenezi zikutheka chifukwa chakuti amapeza “mphamvu kuchokera kwa Ambuye.” Koma pali zinanso zimene amachita. Mofanana ndi asilikali ophunzitsidwa bwino, iwo amakhala okonzeka chifukwa choti amavala “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.” (Aef. 6:10-12) N’kutheka kuti pamene Paulo ankafotokoza fanizo lakeli, ankaganizira zida zankhondo zimene asilikali achiroma ankavala.—Mac. 28:16. w18.05 27 ¶1-2
Lolemba, January 27
Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.—Mat. 6:9.
Chifukwa chachikulu chimene timalalikirira ndi kulemekeza Yehova komanso kuyeretsa dzina lake. (Yoh. 15:1, 8) Koma n’zosatheka kuti tichititse dzina la Mulungu kukhala loyera kuposa mmene lilili. Dzinalo ndi loyera kale kapena kuti lopatulika kwambiri. Koma taonani zimene mneneri Yesaya ananena. Iye anati: “Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera.” (Yes. 8:13) Choncho timayeretsa dzina la Mulungu tikamaliona kuti ndi lapamwamba kwambiri kuposa mayina ena onse komanso tikamathandiza anthu ena kuona kuti ndi loyera. Mwachitsanzo, tikamauza anthu za makhalidwe abwino a Yehova komanso cholinga chake chokhudza anthu chimene sangachisinthe, timasonyeza kuti zimene Satana ananena zokhudza Yehova ndi zabodza. (Gen. 3:1-5) Timayeretsanso dzina la Mulungu tikamathandiza anthu kuzindikira kuti Yehova ndi woyenera “kulandira ulemerero ndi ulemu.”—Chiv. 4:11. w18.05 18 ¶3-4
Lachiwiri, January 28
Ndi bwino kuyamika inu Yehova . . . Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu. Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.—Sal. 92:1, 4.
Chifukwa chachikulu chokhalira ndi zolinga zauzimu n’chakuti timafuna kusonyeza kuti timayamikira chikondi cha Yehova komanso zonse zimene watichitira. Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kuganizira zinthu zambiri zimene Yehova wakupatsani. Mwachitsanzo, wakupatsani moyo, mfundo zimene mumakhulupirira, Baibulo, mpingo komanso chiyembekezo chabwino. Munthu akamaika zinthu zauzimu pamalo oyamba amasonyeza kuti akuyamikira zinthu zonse zimene Mulungu watipatsa ndipo zimathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi wolimba. Komanso munthu akamayesetsa kukwaniritsa zolinga zake amakhala akupanga mbiri yabwino pamaso pa Yehova. Izi zimathandiza kuti ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova uzilimba. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Choncho musaganize kuti ndinu wamng’ono moti simungakhale ndi zolinga zauzimu. Kodi ndi zolinga ziti zimene mungakonde kukhala nazo, nanga mungachite chiyani kuti muzikwaniritse?—Afil. 1:10, 11. w18.04 26 ¶5-6
Lachitatu, January 29
Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.—2 Akor. 3:17.
Anthu a mu ulamuliro wa Aroma ankadziona kuti ndi otsatira kwambiri malamulo komanso amalimbikitsa chilungamo ndi ufulu. Koma Aromawo anali ndi mphamvu komanso ulemerero chifukwa cha ntchito zimene akapolo ankagwira. Pa nthawi ina, anthu atatu pa anthu 10 alionse mu ulamuliro wa Aroma anali akapolo. Choncho n’zosakayikitsa kuti anthu ambiri, ngakhalenso Akhristu akumeneko, ankakonda kukamba za ukapolo ndi ufulu. Nkhani ya ufuluyi imatchulidwatchulidwanso m’makalata a Paulo. Ngakhale kuti m’masiku a Paulo anthu ankakonda kumenyera ufulu wawo, cholinga cha Paulo sichinali chimenecho. M’malo modalira kuti olamulira kapena mabungwe adzabweretsa ufulu, Paulo ndi Akhristu anzake ankayesetsa kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu komanso kufunika kwa nsembe ya dipo imene Khristu Yesu anapereka. Apa tingati iye ankathandiza anthu kuti apeze ufulu weniweni. w18.04 8 ¶1-2
Lachinayi, January 30
Simoni, Simoni! Ndithu Satana akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu. Koma ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.—Luka 22:31, 32.
Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza Petulo mawu ali pamwambawa. Petulo anali ngati mzati mumpingo wachikhristu woyambirira. (Agal. 2:9) Kulimba mtima kumene anasonyeza kuyambira pa Pentekosite kunathandiza Akhristu ena kuti nawonso alimbe mtima. Chakumapeto kwa utumiki wake padzikoli, anauza Akhristu anzake kuti: “Ndakulemberani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kupereka umboni wamphamvu wakuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu.” (1 Pet. 5:12) Makalata amene Petulo analemba analimbikitsa Akhristu kwa zaka zambiri. Mfundo zake n’zolimbikitsanso masiku ano pamene tikuyembekezera kuti malonjezo a Yehova akwaniritsidwe.—2 Pet. 3:13. w18.04 17 ¶12-13
Lachisanu, January 31
Woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita.—Yak. 1:25.
Aliyense amafuna kuti azichita zimene akufuna basi. Koma kodi anthu amatani pofuna kupeza ufulu umenewu? Ambiri amakonda kuukira boma, kupanga zionetsero kapena kuyambitsa mabungwe omenyera ufulu. Koma kodi zimenezi zimathandizadi? Ayi. M’malomwake zimangoyambitsa mavuto ndipo ena amaphedwa poyesa kumenyera ufulu. Zonsezi zikungotsimikizira mfundo imene Solomo analemba m’Baibulo yakuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlal. 8:9) Mulemba la lero, Yakobo anatchula mfundo yofunika imene ingathandize munthu kukhala wosangalala komanso waufulu. Yehova ndi amene anatipatsa lamulo langwiro ndipo amadziwa chimene chingathandize munthu kuti akhale pa ufulu komanso wosangalala. Atalenga anthu oyambirira, anawapatsa chilichonse chimene ankafunikira kuti asangalale ndipo chinthu china chimene anawapatsa ndi ufulu. w18.04 3 ¶1-3