February
Loweruka, February 1
Ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.—2 Tim. 4:5.
Yesu ankaganizira kwambiri anthu ena. Anthu ankachita kuoneratu kuti amawakonda ndipo ankamvetsera uthenga wa Ufumu. Ifenso tikamakonda anthu, ntchito yathu yolalikira iziyenda bwino. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamvera chifundo anthu amene timawalalikira? Tiyenera kuganizira kuti, Kodi ineyo ndikanakhala kuti ndakumana ndi mavuto awowa, ndikanafuna kuti anthu andichitire zotani? Kenako tiziwachitira zimene ifeyo tikanafuna kuchitiridwazo. (Mat. 7:12) Tiziganizira vuto la munthu aliyense. Tisamangofotokoza zinthu zofanana kwa aliyense amene tingakumane naye. M’malomwake, tiziganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthu aliyense komanso maganizo ake. Muzimufunsa mafunso okuthandizani kudziwa maganizo ake. (Miy. 20:5) Tikamafunsa mafunso n’kukambirana ndi anthu zimakhala ngati tikuwalola kutiuza chifukwa chake akufunikira uthenga wabwino. Tikadziwa zimenezi tikhoza kuchitira munthu chifundo n’kumuthandiza m’njira yoyenera ngati mmene Yesu ankachitira.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:19-23. w19.03 20 ¶2; 22 ¶8-9
Lamlungu, February 2
Pereka ntchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.—Miy. 16:3.
Adamu ndi Hava anasonyeza kuti sankayamikira zinthu zabwino zimene Yehova anawachitira. Tonsefe tili ndi mwayi wosonyeza kuti sitigwirizana ndi zimene iwo anasankha. Tikabatizidwa, timasonyeza kuti timavomereza kuti Yehova ndi woyenera kutiuza kuti izi n’zabwino, izi n’zoipa. Timasonyezanso kuti timakonda Yehova komanso kumukhulupirira. Munthu akabatizidwa, nkhani tsopano imakhala yoti aziyendera mfundo za Yehova tsiku lililonse osati zake. Izi n’zimene anthu mamiliyoni ambiri akuchita masiku ano. Nanunso mukhoza kuchita zimenezi. Chinsinsi chake ndi kuyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu, kusonkhana nthawi zonse komanso kuchita khama pouza ena mfundo zokhudza Atate wanu zimene mwaphunzira. (Aheb. 10:24, 25) Mukafuna kusankha zochita, muziganizira malangizo amene Yehova wapereka kudzera m’Mawu ake ndi gulu lake. (Yes. 30:21) Mukamachita zimenezi, zinthu zidzakuyenderani bwino.—Miy. 16:20. w19.03 7 ¶17-18
Lolemba, February 3
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo.—Yak. 1:17.
Yehova watipatsa chakudya chauzimu chamwanaalirenji. Mwachitsanzo, timalandira malangizo kumisonkhano, m’magazini komanso pawebusaiti yathu. Kodi munamvapo nkhani, kuwerenga nkhani kapena kuonera zinthu pa JW Broadcasting® n’kuganiza kuti, ‘Nkhani imeneyi ndiye akonzera ineyotu’? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova? (Akol. 3:15) Njira imodzi ndi kumuthokoza nthawi zonse m’mapemphero athu chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatipatsa. Timasonyezanso kuti timayamikira Yehova tikamaonetsetsa kuti malo athu olambirira ndi aukhondo. Tiyenera kuyeretsa nawo komanso kukonza zinthu m’Nyumba ya Ufumu yathu. Komanso ngati tili ndi udindo wosamalira zipangizo za mpingo monga zokuzira mawu kapena zoonetsera mavidiyo, tiyenera kuzisamalira bwino. Tikamasamalira bwino Nyumba za Ufumu zathu, zinthu sizingawonongeke msanga. Izi zimathandiza kuti pakhale ndalama zomangira kapena kukonzera Nyumba za Ufumu zina padziko lonse. w19.02 18 ¶17-18
Lachiwiri, February 4
Zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake, ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.—Yobu 26:14.
Yobu ankaganizira kwambiri zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga. (Yobu 26:7, 8) Ankagoma kwambiri akaganizira za dziko lapansi, mlengalenga, mitambo komanso mabingu. Koma ankazindikiranso kuti ankangodziwa zochepa zokha zokhudza zinthu zambiri zimene Mulungu analenga. Iye ankayamikiranso kwambiri mawu a Mulungu moti ananena kuti: “Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake.” (Yobu 23:12) Yobu ankalemekeza kwambiri Yehova. Iye ankakonda kwambiri Atate wake ndipo ankafunitsitsa kumusangalatsa. Zimenezi zinamuthandiza kukhala ndi mtima wosagawanika. Tiyenera kutengera chitsanzo chake. Ifeyo timadziwa zambiri zokhudza chilengedwe kuposa zimene anthu ankadziwa nthawi ya Yobu. Komanso tili ndi Baibulo lomwe limatithandiza kudziwa bwino Yehova. Zimene timaphunzira zokhudza Yehova zimatigometsa komanso zimatithandiza kuti tizimulemekeza kwambiri. Tikamachita zimenezi tidzamukonda kwambiri, tidzamumvera komanso tidzakhala ofunitsitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika.—Yobu 28:28. w19.02 5 ¶12
Lachitatu, February 5
Sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?—Sal. 118:6.
Kuyambira kale, olamulira apadzikoli akhala akuzunza anthu a Yehova. Iwo akhoza kutiimba milandu yosiyanasiyana, koma chifukwa chenicheni chimene amatizunzira n’chakuti ‘timamvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’ (Mac. 5:29) Tikhoza kunyozedwa, kumangidwa kapena kuchitiridwa nkhanza zina. Koma Yehova angatithandize kuti tikhalebe odekha n’kumapewa kubwezera. Chitsanzo ndi zimene Hananiya, Misayeli ndi Azariya anachita. Iwo anafotokozera mfumu modekha chifukwa chimene sangalambirire fano limene inapanga. Anyamatawa anali okonzeka kumvera Yehova ngakhale kuti sankadziwa ngati awapulumutse pa nthawiyo. (Dan. 3:1, 8-28) Kodi tingatsanzire bwanji anyamata amenewa tikamayesedwa kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova? Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumadalira Yehova kuti azitisamalira. (Sal. 118:7) Anthu akamatitsutsa tiyenera kuyankha modekha komanso mwaulemu. (1 Pet. 3:15) Tiyeneranso kupewa kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Atate wathu wachikondi. w19.02 10-11 ¶11-13
Lachinayi, February 6
Limbani mtima.—Yoh. 16:33.
Kuti tikhale olimba mtima kwambiri, tiyenera kuganizira zinthu zimene zingatheke chifukwa cha dipo la Khristu. (Yoh. 3:16; Aef. 1:7) Nyengo ya Chikumbutso ikamayandikira timakhala ndi mwayi woganizira zimene Yesu anatichitira n’kumaziyamikira. Choncho, tiyenera kutsatira pulogalamu ya kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso komanso kuganizira kwambiri zimene zinachitika m’masiku otsiriza a moyo wa Yesu padzikoli. Izi zingatithandize kuti tikapita kumwambowu tikamvetse bwino tanthauzo la zizindikiro komanso nsembe yamtengo wapatali imene zimaimira. Tikazindikira zimene Yehova ndi Yesu atichitira n’kumvetsa mmene zimathandizira ifeyo ndi anzathu, chiyembekezo chathu chimakhala champhamvu ndipo zimatilimbikitsa kuti tikhalebe olimba mtima mpaka mapeto. (Aheb. 12:3) Timayamikira kwambiri kuti Yesu adakali wolimba mtima ndiponso wodzichepetsa pamene akugwira ntchito monga Mkulu wa Ansembe amene amatichonderera kwa Mulungu. (Aheb. 7:24, 25) Kuti tisonyeze kuyamikira, tiyenera kutsatira lamulo la Yesu lakuti tizichita mwambo wokumbukira imfa yake.—Luka 22:19, 20. w19.01 22 ¶8; 23-24 ¶10-11
Lachisanu, February 7
Inu Yehova, chonde kondwerani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga.—Sal. 119:108.
Yehova watipatsa tonsefe mwayi womutamanda. Tikamayankha pamisonkhano timakhala kuti tikupereka ‘nsembe zotamanda Mulungu’ ndipo palibe munthu wina amene angatiperekere nsembe zimenezi. (Aheb. 13:15) Kodi Yehova amafuna kuti tonsefe tizipereka nsembe kapena ndemanga zofanana? Ayi. Muziona kuti misonkhano ili ngati chakudya chimene mukudya ndi anzanu apamtima. Tiyerekeze kuti abale ndi alongo akuitanani kuti mukadye nawo chakudya ndipo akupemphani kuti mukonze kachakudya kenakake. Kodi mungatani? Mwina mungade nkhawa pang’ono koma mungayesetse kukonza chakudya chimene aliyense angakonde. Yehova ndi amene amatiitanira kumisonkhano ndipo amatikonzera zinthu zabwino zambiri. (Sal. 23:5; Mat. 24:45) Iye amasangalala tikamabweretsanso mphatso inayake imene tingakwanitse. Choncho tiziyesetsa kukonzekera bwino ndiponso kuyankha mmene tingathere. Tikamachita zimenezi timakhala ngati tikudya patebulo la Yehova komanso tikupereka mphatso kwa onse mumpingo. w19.01 8 ¶3; 13 ¶20
Loweruka, February 8
Zopweteka zimachuluka kwa anthu amene amati akaona mulungu wina, amamuthamangira.—Sal. 16:4.
Kale, anthu akamalambira milungu yonyenga, nthawi zambiri ankachitanso zachiwerewere. (Hos. 4:13, 14) Anthuwo ankakonda kulambira milungu yonyenga chifukwa ankakondanso zachiwerewere. Koma sizinathandize anthu kuti azikhaladi osangalala. Paja Davide ananena kuti “zopweteka zimachuluka kwa anthu” amene amalambira milungu ina. Anthuwo anafikanso pomapereka nsembe ana awo kwa milungu yonyenga. (Yes. 57:5) Yehova ankadana ndi nkhanza zimenezi. (Yer. 7:31) Masiku anonso, zipembedzo zonyenga zimalekerera anthu ochita chiwerewere komanso kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Anthu akamachita zimenezi amaganiza kuti ali pa ufulu koma ‘amangochulukitsa zopweteka zawo.’ (1 Akor. 6:18, 19) Mwina inuyo mwaonapo mavuto amene anthu oterewa amakumana nawo. Choncho achinyamatanu muzimvera Atate wanu wakumwamba. Musamakayikire kuti kumvera Mulungu n’kothandiza kwambiri. Muzikhulupiriranso kuti mavuto amene angabwere mukamachita zoipa ndi ochuluka kwambiri kuposa chisangalalo cha kanthawi chimene mungapeze.—Agal. 6:8 w18.12 27-28 ¶16-18
Lamlungu, February 9
Inenso sindigona nawe.—Hos. 3:3.
Ngati mwamuna kapena mkazi wa Mkhristu angachite dama, Mkhristu wosalakwayo ayenera kusankha zochita. Yesu ananena kuti wosalakwayo ali ndi chifukwa chovomerezeka chothetsera banja n’kukwatira kapena kukwatiwanso. (Mat. 19:9) Komabe akhoza kusankha kukhululukira mwamuna kapena mkazi wakeyo. Kuchita zimenezi si kulakwa. Paja Hoseya anamutenganso Gomeri. Hoseya atamutenganso anamuuza kuti asachitenso dama ndi mwamuna wina. Hoseya sanagone ndi Gomeri kwa kanthawi. (Hos. 3:1-3) Koma kenako ayenera kuti anayambanso kugonana naye. Zimenezi zinasonyeza kuti Mulungu anali wokonzeka kukhululukira anthu ake n’kumachitanso nawo zinthu. (Hos. 1:11; 3:4-5) Kodi mfundo imeneyi ingatithandize bwanji pa nkhani ya ukwati? Ngati Mkhristu wayambanso kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wake yemwe wachita chigololo ndiye kuti akusonyeza kuti wamukhululukira. (1 Akor. 7:3, 5) Akatero sakhalanso ndi ufulu wothetsa banja ndipo ayenera kuthandizana ndi mnzakeyo kuti akhale ndi maganizo a Mulungu pa nkhani ya ukwati. w18.12 13 ¶13
Lolemba, February 10
Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.—Miy. 22:3.
Tikamaphunzira tingachite bwino kuona maganizo a Yehova pa zinthu zimene zingadzatichitikire m’tsogolo. Tikamatero sitingasowe chochita ngati titakumana ndi vuto lina lofunika kuti tisankhe zochita pompopompo. Chitsanzo choyamba ndi cha Yosefe yemwe anakana kugonana ndi mkazi wa Potifara. Zimene Yosefe anachita zimasonyeza kuti anaganiziratu maganizo a Yehova pa nkhani ya kukhulupirika m’banja. (Gen. 39:8, 9) Pamene anamuyankha kuti: “Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” anasonyeza kuti ankayendera maganizo a Yehova. Nanga bwanji ifeyo? Kodi tingatani ngati munthu wina kuntchito wayamba kutikopa? Nanga tingatani ngati munthu watitumizira zinthu zolaula pa foni? Zinthu ngati zimenezi sizingakhale zovuta ngati tikudziwiratu maganizo a Yehova pa nkhanizi ndipo tinasankhiratu zochita. w18.11 25 ¶13-14
Lachiwiri, February 11
Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova.—Hab. 3:18.
Akatswiri ena amaganiza kuti zimene Habakuku analankhula muvesi limeneli zinkatanthauza kuti: “Ndidzadumphadumpha chifukwa chosangalala ndi Ambuye. Ndidzavina mozungulirazungulira chifukwa chosangalala ndi Mulungu.” Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri kwa tonsefe. Yehova watilonjeza zinthu zabwino komanso watitsimikizira kuti sachedwa kukwaniritsa cholinga chake. Uthenga wofunika kwambiri wa Habakuku ndi woti tizidalira kwambiri Yehova. (Hab. 2:4) Kuti tizimudalira kwambiri, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu pochita zinthu izi: (1) Kupemphera nthawi zonse n’kumauza Yehova chilichonse chimene chikutidetsa nkhawa; (2) kutsatira malangizo alionse ochokera m’Mawu a Mulungu kapena gulu lake komanso (3) kuyembekezera Yehova moleza mtima komanso mwachikhulupiriro. Habakuku anachita zinthu zitatu zonsezi. Ngakhale kuti anayamba kulemba buku lake ndi mawu odandaula, anamaliza ndi mawu osonyeza kuti walimba mtima komanso akusangalala. Ifenso tikamachita zimenezi tidzamva ngati Yehova watikumbatira. Zimenezi zingatilimbikitse kwambiri m’dziko lamavutoli. w18.11 17 ¶18-19
Lachitatu, February 12
[Khristu] anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.—2 Akor. 5:15.
Akhristu enieni ali ndi chifukwa chinanso chowachititsa kudziwa kuti Yehova amawakonda. Paja Baibulo limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Nayenso Yesu anasonyeza kuti amatikonda pololera kufa chifukwa cha ife. Ndipotu timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira za chikondi chimene Yesu anatisonyezachi. Mawu a Mulungu amatilonjeza kuti ngakhale ‘chisautso kapena zowawa’ sizingatilekanitse ndi “chikondi cha Khristu.” (Aroma 8:35, 38, 39) Chikondi cha Khristu chimatithandiza kupirira tikamakumana ndi mavuto amene amatitopetsa, kutisokoneza maganizo kapena kutifooketsa mwauzimu. (2 Akor. 5:14) Chikondichi chingatilimbikitse kuti tisamataye mtima ngakhale pamene takumana ndi mavuto aakulu monga ngozi zadzidzidzi, kuzunzidwa, nkhawa kapena kukhumudwa. w18.09 14 ¶8-9
Lachinayi, February 13
Ndidzayenda m’choonadi chanu.—Sal. 86:11.
Kuti tiziyendabe m’choonadi, tiyenera kukhulupirira komanso kumvera mawu onse a Yehova. Tiziona kuti choonadi ndi chofunika kwambiri pa moyo wathu komanso kumachita zinthu zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mofanana ndi Davide, tiyenera kutsimikiza mumtima mwathu kuti tidzapitirizabe kuyenda m’choonadi cha Mulungu. Ngati titapanda kuchita zimenezi, tikhoza kuyamba kuganizira zinthu zomwe tinasiya kuti tipeze choonadi mwinanso kuyamba kuzilakalaka. Koma tiyenera kupitiriza kutsatira mfundo zonse za choonadi. Si bwino kusankha mfundo zina za choonadi zoti tizizitsatira n’kusiya zina. Paja Baibulo limati tiyenera kuyenda “m’choonadi chonse.” (Yoh. 16:13) Kuti tipewe kusiya choonadi pang’onopang’ono tiyenera kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu. Kupanda kusamala, nthawi yathu ikhoza kumangothera pa intaneti, pa TV kapena pa zosangalatsa zina. Zinthu zimene tatchulazi pazokha si zolakwika, koma vuto limakhalapo ngati zikutilepheretsa kupezanso nthawi yokwanira yophunzira patokha kapena yochita zinthu zina zokhudza kulambira. w18.11 10 ¶7-8
Lachisanu, February 14
Ndadzitonthoza ndipo ndakhazika mtima wanga pansi.—Sal. 131:2.
Zinthu zikasintha mosayembekezereka pa moyo wathu tikhoza kuchita mantha komanso kudera nkhawa zam’tsogolo. (Miy. 12:25) Mwina tingavutikenso kuti tivomereze kuti zinthu zasintha. Zimenezi zikatichitikira, kodi tingatani kuti ‘tidzitonthoze komanso kukhazika mtima wathu pansi’? (Sal. 131:1-3) Ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto, tikhoza kulimbikitsidwa ndi “mtendere wa Mulungu” umene umateteza maganizo athu. (Afil. 4:6, 7) Choncho tikakhala ndi nkhawa tizipempha Mulungu kuti atipatse mtendere wake umene ungatithandize kuti tisataye mtima koma tiziyesetsabe kuchita zambiri pomutumikira. Kuwonjezera pa kukhazika mtima wathu pansi, mzimu wa Mulungu ungatichititse kuganizira malemba omwe angatithandize kuti tiziikabe maganizo athu pa kutumikira Yehova.—Yoh. 14:26, 27. w18.10 27 ¶2; 28 ¶5, 8
Loweruka, February 15
Muzilankhulana zoona zokhazokha.—Zek. 8:16.
Pali chinthu china chimene chakhala chikusokoneza kwambiri anthu. Chinthu chake ndi bodza. Munthu amatha kulankhula zinthu zimene akudziwa kuti si zoona n’cholinga choti apusitse mnzake. Koma kodi ndi ndani amene anayambitsa bodza? Mdyerekezi ndi amene anayambitsa ndipo n’chifukwa chake Yesu Khristu anamunena kuti ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Kodi ndi liti pamene ananena bodza loyambirira? Zimenezi zinachitika zaka masauzande angapo zapitazo m’munda wa Edeni. Adamu ndi Hava ankakhala mosangalala m’Paradaiso amene Mulungu anawapatsa. Mdyerekezi ankadziwa kuti Mulungu anali atawauza kuti asadye “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” ndipo akapanda kumvera adzafa. Ndiyeno iye anagwiritsa ntchito njoka n’kuuza Hava bodza loyambirira lakuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”—Gen. 2:15-17; 3:1-5. w18.10 6 ¶1-2
Lamlungu, February 16
Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.—Mat. 5:8.
Kuti tikhale oyera mtima tiyenera kuganizira komanso kulakalaka zinthu zabwino. Kukhala ndi maganizo oyera kumatithandiza kuti tizitumikira Yehova m’njira yoyenera. (2 Akor. 4:2; 1 Tim. 1:5) Popeza ‘palibe munthu angaone Mulungu n’kukhalabe ndi moyo,’ kodi anthu oyera mtima ‘amaona’ bwanji Mulungu? (Eks. 33:20) Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti ‘kuona’ amatanthauzanso ‘kuona m’maganizo, kuzindikira komanso kudziwa.’ Anthu amene amaona Mulungu mumtima mwawo ndi amene amamudziwa bwino komanso kudziwa makhalidwe ake. (Aef. 1:18) Kuwonjezera pa kudziwa makhalidwe a Mulungu, anthu ake ‘amamuona’ akamaona mmene amawathandizira. (Yobu 42:5) Iwo amaonanso mumtima mwawo madalitso amene Mulungu walonjeza anthu amene amayesetsa kukhala oyera n’kumamutumikira mokhulupirika. w18.09 20 ¶13, 15-16
Lolemba, February 17
Nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri. Peza nzeru.—Miy. 4:7.
Munthu akamachita zinthu zoyenera amadalitsidwa. N’zoona kuti munthu amapeza nzeru akadziwa zinthu n’kuzimvetsa koma amasonyeza kuti ndi wanzerudi akamasankha zochita mwanzeru. Paja ngakhale nyerere zimasonyeza kuti ndi zanzeru chifukwa zimasungiratu chakudya choti zidzadye m’tsogolo. (Miy. 30:24, 25) Khristu amatchedwa “nzeru za Mulungu” ndipo nthawi zonse amachita zinthu zosangalatsa Atate wake. (1 Akor. 1:24; Yoh. 8:29) Yehova amasiyanitsa anthu amene amangodziwa zoyenera kuchita ndi amene amachita zoyenerazo. Iye amadalitsa anthu odzichepetsa amene amapirira n’kumachita zimene akudziwa kuti n’zoyenera. (Mat. 7:21-23) Choncho tiyeni tipitirize kuchita zinthu zimene zingatithandize kuti aliyense mumpingo azitumikira Mulungu modzichepetsa. Kutsatira zinthu zimene timadziwa kuti n’zoyenera kumatenga nthawi ndipo pamafunika kuleza mtima. Koma zimasonyeza kuti ndife odzichepetsa ndipo zimathandiza kuti tikhale osangalala panopa mpaka muyaya. w18.09 7 ¶18
Lachiwiri, February 18
Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani . . . osati modziyerekezera ndi munthu wina.—Agal. 6:4.
Mlengi wathu ankafuna kuti anthu angwiro azigwira naye ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Ngakhale kuti panopa anthufe si angwiro, tikhoza kugwirabe ntchito ndi Yehova tsiku lililonse. Mwachitsanzo, timakhala “antchito anzake a Mulungu” tikamalalikira ndiponso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu. (1 Akor. 3:5-9) Ndi mwayi waukulu kwambiri kuti Mlengi wa chilengedwe chonse amationa kuti ndife oyenera kugwira naye ntchito imene iye amaiona kuti ndi yofunika kwambiri. Koma kuwonjezera pa kulalikira ndi kuphunzitsa anthu, palinso njira zina zimene timagwirira ntchito ndi Yehova. Njira zake ndi (1) kuthandiza banja lathu komanso Akhristu anzathu, (2) kukhala ochereza, (3) kudzipereka kugwira nawo ntchito zosiyanasiyana m’gulu lathu komanso (4) kuwonjezera zimene timachita mu utumiki. (Akol. 3:23) Tikamakambirana mfundo za munkhaniyi, musamayerekezere zimene mumachita potumikira Yehova ndi zimene anthu ena amachita. Tizikumbukira kuti anthu amasiyana msinkhu, thanzi, maluso komanso mmene zinthu zilili pa moyo wawo. w18.08 23 ¶1-2
Lachitatu, February 19
Uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.—Hab. 2:3.
Yehova anatsimikizira Habakuku kuti mayankho a mafunso ake adzapezeka. Anamuuzanso kuti mavutowo atha pasanapite nthawi yaitali. Apa tingati Yehova anauza mneneriyu kuti: “Tangoleza mtima ndipo uzindikhulupirira. Ndiyankha mafunso akowo ngakhale kuti zikuoneka ngati ndikuchedwa.” Yehova anakumbutsa Habakuku kuti iye ali ndi nthawi yoyenera kukwaniritsa malonjezo ake. Anamuuza kuti ayenera kuyembekezera kuti aone mmene Yehovayo akwaniritsire zolinga zake. Pamapeto pake, mneneriyo sadzanong’oneza bondo. Kuyembekezera Yehova moleza mtima komanso kumvetsera mawu ake kumatithandiza kuti tikhale olimba mtima komanso odekha pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto. Yesu anatsindikanso ubwino wokhulupirira Yehova podziwa kuti amachita zinthu pa nthawi yake, osati kumangoganizira za “nthawi kapena nyengo” zimene Yehovayo sanaulule panopa. (Mac. 1:7) Choncho tiyeni tisataye mtima koma tiziyembekezera Yehova modzichepetsa, mwachikhulupiriro komanso moleza mtima. Tizigwiritsa ntchito nthawi imene tili nayo potumikira Yehova ndi moyo wathu wonse.—Maliko 13:35-37; Agal. 6:9. w18.11 16 ¶13-14
Lachinayi, February 20
Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti woipitsidwa kapena wonyansa.—Mac. 10:28.
Mofanana ndi Ayuda ena a pa nthawiyo, Petulo anakula akukhulupirira kuti anthu a mitundu ina anali odetsedwa. Koma zinthu zimene zinamuchitikira zinamuchititsa kusintha maganizo amenewa. (Mac. 10:9-16) Ifenso tiyenera kudzifufuza kwambiri komanso kukhala ololera kuthandizidwa n’cholinga choti tichotseretu kamtima kalikonse katsankho kamene tatsala nako. Kodi n’chiyaninso chimene tingachite? Tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi chikondi mumtima mwathu m’malo mwa tsankho. (2 Akor. 6:11-13) Ndi bwino kudzifunsa kuti, Kodi ndimakonda kumangocheza ndi anthu amtundu wanga, dziko langa, fuko langa kapena chilankhulo changa? Ngati zili choncho, tiyenera kusintha mtima wathu. Tingachite bwino kumaitana anthu osiyana ndi ifeyo kuti tidzadyere limodzi, tidzacheze nawo kapena kulowa nawo mu utumiki. (Mac. 16:14, 15) Tikamatero, chikondi chidzawonjezeka kwambiri mumtima mwathu moti simudzakhalanso malo oti tsankho lipezekemo. w18.08 9 ¶3, 6; 10 ¶7
Lachisanu, February 21
Pewani kukhala okhumudwitsa.—1 Akor. 10:32.
Pali zinthu zinanso zimene a Mboni ena amachita potsanzira anthu a m’dzikoli. Mwachitsanzo, amavina komanso kuchita zinthu zina pamapwando zomwe si zoyenera Akhristu. Komanso amaika zithunzi zawo ndiponso kulemba zinthu zina pa intaneti zomwe n’zosayenera kwa Akhristu enieni. Iwo akhoza kusokoneza kwambiri anthu amene amafuna kukhala ndi khalidwe labwino potumikira Yehova. (1 Pet. 2:11, 12) Dzikoli limalimbikitsa kwambiri “chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Koma popeza tinadzipereka kwa Yehova, timalimbikitsidwa kuti tizikana “moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.” (Tito 2:12) Choncho mawu athu komanso zimene timachita pa nkhani ya kudya, kumwa, kuvala ndi kudzikongoletsa ziyenera kusonyezeratu anthu ena kuti tinadzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse. w18.07 25 ¶13-14
Loweruka, February 22
Maso athu adzayang’ana kwa Yehova Mulungu wathu, kufikira atatikomera mtima.—Sal. 123:2.
Ngati timayang’ana kwa Yehova nthawi zonse, sitidzalola kuti zochita za anthu ena zitikwiyitse kapena zisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova. N’zoona kuti tonsefe tiyenera ‘kukonza chipulumutso chathu, mwamantha ndi kunjenjemera.’ (Afil. 2:12) Koma tizikumbukira kuti Yehova saweruza tchimo lililonse mofanana. Iye amayembekezera zambiri kwa anthu amene ali ndi udindo ngati mmene zinalili ndi Mose. (Luka 12:48) Ngati timakonda Yehova ndi mtima wonse, sitidzalola chilichonse kutipunthwitsa kapena kutisiyanitsa ndi chikondi chake. (Sal. 119:165; Aroma 8:37-39 M’masiku ovuta ano, tiyenera kuyesetsa kuti nthawi zonse tiziyang’ana kwa ‘amene akukhala kumwamba’ n’cholinga choti tidziwe zimene akufuna kuti tichite. (Sal. 123:1) Tisalole kuti ubwenzi wathu ndi Yehova usokonezedwe ndi zochita za anthu ena. w18.07 16 ¶19-20
Lamlungu, February 23
Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, . . . kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.—Mat. 5:16.
Timasangalala tikamamva mmene anthu a Yehova akuchulukira. Mwachitsanzo, mu 2017, tinachititsa maphunziro a Baibulo oposa 10,000,000. Izi zikusonyeza kuti atumiki a Mulungu akuonetsadi kuwala kwawo. Ndipo panali anthu achidwi mamiliyoni ambiri amene anapezeka pa Chikumbutso. Iwo anakhala ndi mwayi wophunzira mmene Mulungu anasonyezera chikondi popereka nsembe ya Yesu. (1 Yoh. 4:9) Anthu a Yehova padziko lonse amalankhula zilankhulo zosiyanasiyana. Koma izi sizimatilepheretsa kuti tizilambira Atate wathu, Yehova, mogwirizana. (Chiv. 7:9) Ngakhale kuti timalankhula zilankhulo zosiyana komanso timakhala kosiyana, tonsefe tikhoza kuwala “monga zounikira m’dzikoli.” (Afil. 2:15) Zinthu monga kukula kwa gulu lathu, mgwirizano umene tili nawo komanso kukhalabe maso kwathu, zimathandiza kuti Yehova alemekezeke. w18.06 21 ¶1-3
Lolemba, February 24
Rabi, idyani.—Yoh. 4:31.
Yankho la Yesu linasonyeza kuti maganizo ake onse anali pophunzitsa mkaziyo moti sankaganiza za njala. Cholinga cha Atate wake chinali choti azilalikira ngakhale kwa akazi achisamariya, moti kuchita zimenezi ankaona ngati kudya chakudya. (Yoh. 4:32-34) Koma Yakobo ndi Yohane sanaphunzirepo. Yesu ndi ophunzira ake akuyenda ku Samariya anapempha malo ogona pamudzi winawake. Asamariyawo atawakaniza malo ogona, Yakobo ndi Yohane anakwiya n’kunena kuti m’pofunika kuwaitanira moto kumwamba kuti uwononge mudzi wonsewo. Koma Yesu anawadzudzula mwamphamvu. (Luka 9:51-56) Koma kodi Yakobo ndi Yohane akananena zimenezi zikanakhala kuti amene akaniza malowo ndi anthu akwawo ku Galileya? Zikuoneka kuti mtima watsankho ndi umene unawachititsa kuti akwiyire kwambiri anthuwo. Patapita nthawi Yohane anapita ku Samariya n’kupeza kuti anthu ambiri ankafuna kumva uthenga wabwino ndipo n’kutheka kuti anachita manyazi ndi zomwe ananena zija.—Mac. 8:14, 25. w18.06 10-11 ¶12-13
Lachiwiri, February 25
Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi m’chiuno mwanu.—Aef. 6:14.
Tikamadziwa bwino komanso kukonda mfundo zoona zopezeka m’Baibulo, zimakhala zosavuta kuzitsatira pa moyo wathu komanso kunena zoona nthawi zonse. Tikutero chifukwa chakuti Satana ndi amene wakhala akugwiritsa ntchito mabodza popusitsa anthu. Munthu amene amanena mabodza komanso amene amawakhulupirira amakumana ndi mavuto. (Yoh. 8:44) Choncho ngakhale kuti si ife angwiro, tiyenera kuyesetsa kupewa bodza. (Aef. 4:25) Koma kuchita zimenezi si kophweka. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Abigail anati: “Nthawi zina kunena zoona kungaoneke ngati kosathandiza. Izi zingachitike makamaka pamene kunama kungakuthandize kuti usakumane ndi vuto linalake.” Ndiye n’chifukwa chiyani tiyenera kunena zoona? Mtsikana wina wazaka 23 dzina lake Victoria anati: “N’zoona kuti ukamanena zoona komanso kufotokozera anthu zimene umakhulupirira, ena angakuvutitse. Koma pali ubwino wake. Munthu akamanena zoona amasiya kudzikayikira, amalimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova komanso anzake amamulemekeza.” Mosakayikira, ‘kumanga kwambiri choonadi m’chiuno mwathu’ nthawi zonse n’kothandiza kwambiri. w18.05 28 ¶3, 5
Lachitatu, February 26
Khalanibe maso.—Mat. 24:42.
Tonsefe tikufunika kukhalabe maso pamene zinthu zikuipiraipira m’dzikoli. Ndipo mapeto a dzikoli sadzalephera kufika pa nthawi imene Yehova anasankha. (Mat. 24:42-44) Pakali pano tikufunika kukhala oleza mtima komanso kukhalabe maso. Tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndiponso tizipemphera nthawi zonse. (1 Pet. 4:7) Tizitengera chitsanzo cha abale ndi alongo amene akhalabe maso kwa nthawi yaitali ndipo akuonetsabe kuwala kwawo. Muzikhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova komanso muzicheza ndi abale ndi alongo amene angakulimbikitseni. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukhale wosangalala komanso musamaone kuti nthawi ikuchedwa. (Aef. 5:16) N’zolimbikitsa kuti Yehova amatilolabe kuti tizimutumikira ngakhale kuti si ife angwiro. Ndi bwino kuti tiziyamikira akulu omwe ndi “mphatso za amuna” zimene Yehova anatipatsa. (Aef. 4:8, 11, 12) Choncho mkulu wina akadzakuyenderani, mudzagwiritse ntchito mwayi umenewo kuti mupindule ndi nzeru komanso malangizo ake. w18.06 24-25 ¶15-18
Lachinayi, February 27
Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa.—Yoh. 15:10.
Yesu sanangouza ophunzira ake kuti amukonde koma anati ‘akhalebe m’chikondi chake.’ Ananena zimenezi chifukwa chakuti munthu amafunika kupirira kuti chaka chilichonse moyo wake uzisonyeza kuti ndi wophunzira weniweni wa Khristu. Pa Yohane 15:4-10, Yesu anagwiritsa ntchito mobwerezabwereza mawu osonyeza kuchita zinthu mopitiriza pofuna kutsindika mfundo yoti kupirira n’kofunika. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timafunitsitsa kusangalatsa Khristu komanso kukhalabe m’chikondi chake? Chofunika n’kutsatira malamulo ake. Mwachidule tingati Yesu akungotiuza kuti, ‘Muzindimvera.’ Zimene Yesu anatiuza kuchita n’zimene iyenso amachita. Paja atauza ophunzira ake kuti azisunga malamulo ake anapitiriza kuti: “Monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.” Choncho tinganene kuti Yesu anatipatsa chitsanzo. (Yoh. 13:15) Tikamamvera lamulo la Yesu loti tizilalikira, timasonyezanso kuti timakonda Mulungu chifukwa malamulo a Yesu amakhala ogwirizana ndi maganizo a Atate wake. (Mat. 17:5; Yoh. 8:28) Tikamasonyeza kuti timakonda Yehova ndi Yesu, iwonso amapitiriza kutikonda. w18.05 18 ¶5-7
Lachisanu, February 28
Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.—Miy. 21:5.
Achinyamata amafunika kusankha zochita pa nkhani monga maphunziro, ntchito komanso zinthu zina. Munthu amene akudziwa zolinga zimene ali nazo savutika kusankha zochita. Choncho munthu akakhala ndi zolinga adakali wamng’ono zinthu zimamuyendera bwino mwamsanga. M’mipingo yambiri muli achinyamata amene akuchita bwino ndipo ayenera kuyamikiridwa kwambiri. Iwo anadzipereka kwa Yehova ndipo akuyesetsa kukwaniritsa zolinga zawo zauzimu. Achinyamatawa amasangalala komanso amaphunzira kutsatira mfundo za Yehova pa zonse zimene amachita, kuphatikizapo pa nkhani zokhudza banja. Paja Mfumu Solomo analemba kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miy. 3:5, 6) Achinyamata m’mipingo yachikhristu ndi amtengo wapatali pamaso pa Yehova ndipo Yehovayo amawakonda kwambiri, kuwateteza, kuwatsogolera komanso kuwadalitsa. w18.04 26 ¶7; 27 ¶9
Loweruka, February 29
Muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana.—Yoh. 13:34.
Mtumwi Yohane anali mzati mumpingo wachikhristu woyambirira. Uthenga wabwino wonena za Yesu umene analemba unalimbikitsanso Akhristu kwa zaka zambiri ndipo umatilimbikitsanso masiku ano. Mwachitsanzo, mfundo imene Yesu ananena yoti chikondi ndi chizindikiro cha Akhristu enieni imapezeka mu uthenga wake wokha. (Yoh. 13:35) Makalata atatu amene Yohane analemba alinso ndi mfundo zachoonadi zolimbikitsa. Mwachitsanzo, ngati tikudziimba mlandu pa machimo amene tinachita, timalimbikitsidwa kwambiri tikawerenga mawu ake akuti “magazi a Yesu . . . akutiyeretsa ku uchimo wonse.” (1 Yoh. 1:7) Ndipo ngati mtima wathu ukupitiriza kutitsutsa, umakhala m’malo ndipo timayamba kumva bwino tikawerenga mawu akuti: “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (1 Yoh. 3:20) Pajanso Yohane yekha ndi amene analemba kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8, 16) Kalata yake yachiwiri ndi yachitatu imayamikira Akhristu amene amapitiriza ‘kuyenda m’choonadi.’—2 Yoh. 4; 3 Yoh. 3, 4. w18.04 18 ¶14-15