Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es21
  • February

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • February
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2021
  • Timitu
  • Lolemba, February 1
  • Lachiwiri, February 2
  • Lachitatu, February 3
  • Lachinayi, February 4
  • Lachisanu, February 5
  • Loweruka, February 6
  • Lamlungu, February 7
  • Lolemba, February 8
  • Lachiwiri, February 9
  • Lachitatu, February 10
  • Lachinayi, February 11
  • Lachisanu, February 12
  • Loweruka, February 13
  • Lamlungu, February 14
  • Lolemba, February 15
  • Lachiwiri, February 16
  • Lachitatu, February 17
  • Lachinayi, February 18
  • Lachisanu, February 19
  • Loweruka, February 20
  • Lamlungu, February 21
  • Lolemba, February 22
  • Lachiwiri, February 23
  • Lachitatu, February 24
  • Lachinayi, February 25
  • Lachisanu, February 26
  • Loweruka, February 27
  • Lamlungu, February 28
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2021
es21

February

Lolemba, February 1

[Yehova] amakonda chilungamo.​—Sal. 33:5.

M’Baibulo, mawu akuti “chilungamo” amatanthauza kuchita zinthu zimene Mulungu amaziona kuti ndi zabwino, komanso kuzichita mosakondera. Taganizirani mmene zochita za Yesu zimasonyezera kuti amakonda chilungamo. Pa nthawi imene iye anali padzikoli, atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda ankadana ndi anthu amitundu ina, ankanyoza Ayuda wamba komanso sankalemekeza akazi. Koma Yesu ankachita zinthu ndi anthu onse mwachilungamo komanso mosakondera. Iye ankalandira anthu omwe sanali Ayuda amene ankamukhulupirira. (Mat. 8:5-10, 13) Ankalalikira mosakondera kwa anthu onse, kaya achuma kapena osauka. (Mat. 11:5; Luka 19:2, 9) Iye sankachitira nkhanza akazi, koma ankachita nawo zinthu mwaulemu ndiponso mokoma mtima. Ankachita zimenezi ngakhale kwa akazi amene anthu ena ankawanyoza. (Luka 7:37-39, 44-50) Tingatsanzire Yesu tikamachita zinthu mosakondera. Tiyenera kulalikiranso munthu aliyense amene akufuna kumvetsera ndipo sitiyenera kuganizira za chuma chake kapena chipembedzo chake. Amuna a Chikhristu amatsatira chitsanzo cha Yesu akamachita zinthu mwaulemu ndi akazi. w19.05 2 ¶1; 5 ¶15-17

Lachiwiri, February 2

Tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira ana ake.​—1 Ates. 2:7.

Masiku anonso, akulu ayenera kukhala odekha komanso kusankha bwino mawu akamalimbikitsa anthu pogwiritsa ntchito Malemba. Kodi ndi akulu okha amene angalimbikitse anthu amene anagwiriridwa? Ayi. Tonsefe tili ndi udindo woti ‘tizilimbikitsana.’ (1 Ates. 4:18) Alongo olimba mwauzimu angalimbikitse kwambiri alongo ena amene akuvutika. M’pake kuti Yehova Mulungu ananena kuti iye ali ngati mayi amene amatonthoza mwana wake. (Yes. 66:13) M’Baibulo muli zitsanzo za akazi amene analimbikitsa anzawo. (Yobu 42:11) Yehova amasangalala kwambiri akamaona alongo amene amalimbikitsa alongo anzawo omwe akuda nkhawa. Nthawi zina, akulu angapemphe mwachinsinsi mlongo wina wolimba mwauzimu kuti athandize mlongo amene akuvutika maganizo. Tonsefe timadziwa kuti si bwino kulowerera nkhani zimene Mkhristu wina safuna kuti ena azidziwe.​—1 Ates. 4:11. w19.05 16-17 ¶10-12

Lachitatu, February 3

Nkhani [iliyonse imatsimikizika] ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.​—Mat. 18:16.

N’chifukwa chiyani payenera kukhala mboni ziwiri akulu asanakonze zoweruza nkhani kumpingo? Zimenezi zimagwirizana ndi mfundo zachilungamo zopezeka m’Baibulo. Ngati munthu sakuvomereza kuti wachita tchimo, payenera kukhala mboni ziwiri kuti akulu akonze zoweruza nkhaniyo. (Deut. 19:15; 1 Tim. 5:19) Munthu akakana kuti wachita tchimo, akulu ayenera kumva zimene mboni zina zikunena. Ngati pali mboni ziwiri, akulu akhoza kukonza komiti yoweruza. Mboni yoyamba ikhoza kukhala munthu amene wanena za nkhaniyi ndipo yachiwiri ikhoza kukhala munthu angatsimikizire kuti wachitadi tchimo. Koma ngati palibe mboni yachiwiri sizitanthauza kuti mboni yoyambayo sikunena zoona. Ngakhale zitakhala kuti mboni yachiwiri palibe, akulu ayenera kuzindikira kuti mwina munthuyo wachitadi tchimo lalikulu. Akulu ayenera kupitiriza kulimbikitsa anthu onse amene apwetekedwa ndi nkhaniyo komanso kukhala tcheru n’cholinga choti ateteze mpingo.​—Mac. 20:28. w19.05 11 ¶15-16

Lachinayi, February 4

Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama . . . kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.—1 Tim. 4:15.

Ndi bwino kuthandiza ana kuti azidziwa mmene angaphunzirire. Mwachitsanzo, mungawaphunzitse kukonzekera misonkhano kapena kufufuza nkhani yokhudza zimene zachitika kusukulu. (Aheb. 5:14) Ngati ana amaphunzira kunyumba, sangavutike kumvetsera kumisonkhano ya mpingo kapena ikuluikulu. Kuchuluka kwa nthawi imene tingachite kulambirako kumadalira msinkhu wa ana komanso mmene anawo alili. Anthu amene timaphunzira nawo Baibulo amafunikanso kudziwa mmene angaphunzirire paokha. Munthu akangoyamba kuphunzira, timasangalala kumuona akulemba mizere kunsi kwa mayankho pokonzekera phunziro lake kapena misonkhano. Koma tiyenera kuwaphunzitsanso mmene angaphunzirire kapena kufufuza zinthu paokha. Ubwino wa zimenezi ndi wakuti akakumana ndi vuto, sangavutike kufufuza okha m’mabuku zoyenera kuchita. w19.05 26 ¶2; 28 ¶10-11

Lachisanu, February 5

Tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu.​—2 Akor. 10:5.

Tisaiwale kuti cholinga cha Satana ndi kusintha maganizo athu. Iye amagwiritsa ntchito maganizo alionse olakwika kuti tisiye kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. Njira imene amagwiritsa ntchito ndi imene anaigwiritsa ntchito polankhula ndi Hava m’munda wa Edeni. Paja anamufunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati . . . ?” (Gen. 3:1) M’dziko la Satanali, nthawi zambiri timakumana ndi mafunso ngati akuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu amadana ndi ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha? N’zoona kuti Mulungu safuna kuti muzikondwerera khirisimasi ndi tsiku lobadwa? N’zoona kuti Mulungu wanu safuna kuti muziikidwa magazi kuchipatala? N’zoona kuti Mulungu wachikondi angakuletseni kucheza ndi anzanu amene achotsedwa?’ Kuti zitiyendere bwino, tiyenera kutsimikizira kuti zimene timakhulupirira n’zoona. Ngati sitinapeze mayankho abwino pa mafunso amene timakhala nawo mumtima, tikhoza kuyamba kukayikira. Mtima wokayikirawo ukhoza kusokoneza maganizo athu komanso kuwononga chikhulupiriro chathu. w19.06 12-13 ¶15-17

Loweruka, February 6

Nonsenu mukhale amaganizo amodzi, omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu, ndiponso amaganizo odzichepetsa.​—1 Pet. 3:8.

Yehova amatikonda kwambiri. (Yoh. 3:16) Popeza timafuna kumutsanzira, timayesetsa kumvera ena chisoni, kukhala achikondi, komanso achifundo chachikulu. Timasonyeza makhalidwewa makamaka kwa “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” (Agal. 6:10) M’bale kapena mlongo akakumana ndi mavuto timafunitsitsa kumuthandiza. Koma kodi tingalimbikitse bwanji munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira? Choyamba, tiyenera kulankhula ndi munthuyo ngakhale kuti zingativute kupeza mawu abwino omuuza. Paula, yemwe mwamuna wake anamwalira mwadzidzidzi, ananena kuti: “Ndikudziwa kuti anthu amavutika kulankhula ndi munthu yemwe waferedwa. Iwo amaopa kuti zimene anganene zingamukhumudwitse. Koma bola kumva mawu alionse amene anganenedwe kusiyana ndi kuti anthu azingokuyang’ana.” Munthu woferedwa sangayembekezere kuti tinene mawu anzeru kwambiri. Paula anati: “Ndinkayamikira anzanga akangonena kuti, ‘Pepani kwambiri chifukwa cha mavutowa.’” w19.06 20 ¶1; 23 ¶14

Lamlungu, February 7

Yehova, imvani mmene akutiopsezera, ndipo lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.​—Mac. 4:29.

Ngati ntchito yathu italetsedwa, akulu adzakonza zoti muzisonkhana m’njira yoti adani athu asamazindikire. Mwina angakuuzeni kuti muzisonkhana m’timagulu ndipo akhoza kumasinthasintha nthawi komanso malo oti musonkhane. Ntchito yolalikira ikhoza kugwiridwa mosiyanasiyana malinga ndi kumene mumakhala. Koma popeza tonsefe timakonda Yehova ndipo timakonda kuuza anthu za Ufumu wake, tidzapeza njira yoti tizilalikirabe. (Luka 8:1) Wolemba mbiri yakale dzina lake Emily B. Baran anafotokoza zimene a Mboni za Yehova ankachita ku Soviet Union. Iye anati: “Boma litauza a Mboni kuti asiye kulalikira, ankalalikira pocheza ndi anthu amene ankakhala nawo pafupi, anzawo akuntchito komanso anzawo ena. Zimenezi zinachititsa kuti atsekeredwe m’ndende koma a Mboniwo ankalalikirabe kwa akaidi anzawo.” Abale athuwa sanasiye kulalikira ngakhale ntchito yathu italetsedwa. Tiyeni tiziyesetsa kutsatira chitsanzo cha abalewa. w19.07 11 ¶12-13

Lolemba, February 8

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.​—Mat. 28:19.

Kodi tingathandize bwanji anthu amene sakonda zachipembedzo kuti ayambe kukonda Mulungu komanso kukhala ophunzira a Khristu? Tiyenera kuzindikira kuti zimene munthu angachite atamva uthenga wathu zingadalire kumene anakulira. Mwachitsanzo, anthu amene amachokera ku Europe akhoza kuchita zinthu mosiyana ndi anthu a ku Asia. Tikutero chifukwa chakuti ku Europe, anthu ambiri anamvapo zinthu zina zokhudza Baibulo komanso mfundo yoti Mulungu analenga zinthu zonse. Koma ku Asia, anthu ambiri sadziwa za Baibulo komanso sakhulupirira kuti kuli Mlengi. Choncho tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera. Chaka ndi chaka, anthu amene sanali m’chipembedzo chilichonse amakhala a Mboni za Yehova. Ambiri mwa anthuwa amakhala kuti anali kale ndi makhalidwe abwino komanso ankanyansidwa ndi chinyengo cha m’zipembedzo. Pomwe ena anali ndi makhalidwe oipa ndipo ankafunika kusintha. Sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatithandiza kupeza anthu omwe ali ndi ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’​—Mac. 13:48; 1 Tim. 2:3, 4. w19.07 20-21 ¶3-4

Lachiwiri, February 9

Sitikubwerera m’mbuyo.—2 Akor. 4:16.

Kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, tiyenera kuyesetsabe kuti tidzapeze mphotoyi. Mulimonse mmene zilili pa moyo wathu, sitiyenera kuyang’ana zinthu zam’mbuyo kapena kulola chilichonse kuti chitilepheretse kutumikira Yehova mokhulupirika. (Afil. 3:16) N’kutheka kuti zinthu zimene tinkayembekezera sizikuchitika, apo ayi tikudwala kapena takalamba. Mwinanso takhala tikukumana ndi mavuto kapena kuzunzidwa kwa zaka zambiri. Ngakhale zili choncho, ‘tisamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.’ Koma tizingopemphera kwa Mulungu mopembedzera ndipo iye adzatipatsa mtendere umene umaposa chilichonse chimene tingaganizire. (Afil. 4:6, 7) Mofanana ndi wothamanga amene amayesetsa kuthamanga kwambiri akatsala pang’ono kumaliza mpikisano, tiyeni tiziyesetsa kuti timalize mpikisano wathu wokapeza moyo. Tizichita zonse zimene tingathe mogwirizana ndi mmene zilili pa moyo wathu kuti tikapeze mphoto yathu yabwino kwambiri. w19.08 7 ¶16-17

Lachitatu, February 10

Lirani ndi anthu amene akulira.—Aroma. 12:15.

Nthawi zina tikakhala ndi munthu amene waferedwa timasowa chonena. Koma tizikumbukira kuti akangotiona tikulira zimawathandiza kudziwa kuti timawaganizira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Yesu anachita Lazaro atamwalira. Mariya, Marita ndi anthu ena ankalira. Patapita masiku 4, Yesu anafika ndipo nayenso anagwetsa misozi. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa kuti amuukitsa Lazaro pasanapite nthawi yaitali. (Yoh. 11:17, 33-35) Kulira kwa Yesu kunasonyeza mmene Yehova anamveranso Lazaro atamwalira. Zimene anachitazi zinalimbikitsa kwambiri Mariya ndi Marita chifukwa anazindikira kuti iye amawakonda kwambiri. Abale athunso akazindikira kuti timawaganizira komanso kuwakonda, amadziwa kuti sali okha koma ali ndi anzawo amene angawathandize. Nthawi zina tiyenera kungomvetsera pamene akulankhula. Tiyenera kulola m’bale wathu amene waferedwa kufotokoza zimene zili mumtima mwake ndipo tisamakhumudwe ngati akulankhula “zopanda pake.” (Yobu 6:2, 3) Tikutero chifukwa choti munthuyo akhoza kukhala atapanikizika ndi zochita za achibale ake omwe si Mboni. Choncho tiyenera kupemphera naye. Tizipempha “Wakumva pemphero” kuti amupatse mphamvu komanso nzeru.​—Sal. 65:2. w19.04 18-19 ¶18-19

Lachinayi, February 11

Mukhuthulireni za mumtima mwanu.​—Sal. 62:8.

Kaya tikuchita utumiki wa pa Beteli kapena utumiki wina, timayamba kukonda anthu komanso dera limene tikukhala. Koma ngati tikufunika kusiya utumikiwo, zingatipweteke mumtima. Timasowana ndi abale amene tawasiya ndipo ngati tachoka chifukwa chozunzidwa timadera nkhawa abale athuwo. (Mat. 10:23; 2 Akor. 11:28, 29) Tikapatsidwa utumiki watsopano kapena kusiya utumiki n’kubwerera kwathu mwina tingafunike kuzolowera chikhalidwe chakuderalo. Anthu ena amene utumiki wawo wasintha amakumana ndi mavuto azachuma. Zikatero angayambe kuchita mantha komanso kukhumudwa. Kodi n’chiyani chingawathandize? Musasiye kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Yak. 4:8) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kudalira Yehova n’kumakumbukira kuti iye ndi “Wakumva pemphero.” (Sal. 65:2) Yehova “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Sikuti amangochita zimene timamupempha. Koma akhoza kuthetsa mavuto athu m’njira imene sitinkayembekezera kapena kuiganizira. w19.08 21 ¶5-6

Lachisanu, February 12

Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene . . . amatchedwa Haramagedo.​—Chiv. 16:16.

Anthu ena amatchula mawu oti “Aramagedo” ponena za nkhondo yanyukiliya kapena zinthu zina zoopsa. Koma zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Aramagedo n’zabwino komanso zosangalatsa. (Chiv. 1:3) Nkhondo imeneyi ndi yabwino chifukwa idzapulumutsa anthu pothetsa maboma a anthu. Nkhondo imeneyi idzapha anthu oipa onse n’kusiya olungama okhaokha. Idzatetezanso dzikoli kuti lisawonongeke. (Chiv. 11:18) Mawu akuti “Aramagedo,” kapena kuti “Haramagedo,” amapezeka kamodzi kokha m’Malemba ndipo amachokera ku mawu a Chiheberi omwe amatanthauza “Phiri la Megido.” (Chiv. 16:16; mawu am’munsi) Megido unali mzinda wa ku Isiraeli wakale. (Yos. 17:11) Koma Aramagedo si dzina la malo enaake padzikoli. Mawuwa kwenikweni amanena za nthawi pamene “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhanitsidwe kuti alimbane ndi Yehova.​—Chiv. 16:14. w19.09 8 ¶1-3

Loweruka, February 13

Palibe aliyense amene anatha kum’chiritsa.​—Luka 8:43.

Mayi ameneyu ankafuna kwambiri kuthandizidwa. Iye anadwala kwa zaka 12, ndipo anali atapita kwa madokotala osiyanasiyana koma sanamuchiritse. Mogwirizana ndi Chilamulo, mayiyu anali wodetsedwa. (Lev. 15:25) Kenako anamva kuti Yesu akhoza kuchiritsa anthu odwala ndipo anapita kwa iye. Atamupeza n’kugwira chovala chake, anachira nthawi yomweyo. Apatu Yesu anamuthandiza kuti achire komanso kuti azimva kuti amakondedwa ndiponso kulemekezedwa. Mwachitsanzo, polankhula naye anagwiritsa ntchito mawu akuti “mwanawe,” omwe m’chilankhulo chawo ankasonyeza ulemu komanso chikondi. N’zosachita kufunsa kuti mayiyu analimbikitsidwa kwambiri. (Luka 8:44-48) Nkhaniyi imati mayiyo ndi amene anapita kwa Yesu osati anangokhala n’kumamudikira. Ndi mmene zililinso masiku ano. Tiyenera kuyesetsa kuti tipite kwa Yesu. N’zoona kuti panopa, Yesu sachiritsa matenda enieni a anthu amene apita kwa iye. Koma akuitanabe anthu kuti: ‘Bwerani kwa ine ndipo ndidzakutsitsimutsani.’​—Mat. 11:28. w19.09 20 ¶2-3

Lamlungu, February 14

Ndinaona khamu lalikulu . . . lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.—Chiv. 7:9.

Mneneri Zekariya analoseranso zofanana ndi zimenezi. Iye analemba kuti: “M’masiku amenewo, amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zek. 8:23) A Mboni za Yehova amadziwa kuti anthu ochokera m’zilankhulo zonse akhoza kusonkhanitsidwa pokhapokha ngati uthenga wabwino ukulalikidwa m’zilankhulo zambiri. Masiku ano mabuku athu akumasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa m’mbuyo monsemu. Tingati Yehova akuchita zinthu zodabwitsa kwambiri posonkhanitsa khamu lalikulu lochokera m’mitundu yonse. Popeza mabuku ophunzirira Baibulo akupezeka m’zilankhulo zambirimbiri, khamu lalikulu la anthu ochokera kosiyanasiyana likulambira Yehova mogwirizana. Ndipo anthu ake amadziwika chifukwa cha kulalikira mwakhama komanso kukondana. Kunena zoona, zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri.​—Mat. 24:14; Yoh. 13:35. w19.09 30-31 ¶16-17

Lolemba, February 15

Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.​—Mat. 24:21.

Pa nthawi ya chisautso chachikulu, anthu adzadabwa kwambiri kuona zinthu zimene ankaganiza kuti ndi zokhalitsa zitayamba kusokonekera. Iwo adzasowa mtengo wogwira ndipo adzaona kuti moyo wawo uli pa ngozi. (Zef. 1:14, 15) Pa nthawi imeneyo, zinthu ziyenera kuti zidzakhala zovuta ngakhale kwa anthu a Yehova. Popeza timapewa kukhala mbali ya dzikoli, tidzakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ndipo mwina tidzafika posowa zinthu zina zofunika. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakhala akutithandiza kuti tidzakhalebe okhulupirika pa nthawi ya chisautso chachikulu. (Mat. 24:45) Mwachitsanzo, wachita zimenezi pogwiritsa ntchito misonkhano yachigawo ya 2016 mpaka 2018. Pa misonkhano imeneyi, tinalimbikitsidwa kuti tikhale ndi makhalidwe amene angatithandize kuti tidzapulumuke pa tsiku la Yehova. w19.10 14 ¶2; 16 ¶10; 17 ¶12

Lachiwiri, February 16

Sizingatheke kuti muzidya “patebulo la Yehova” komanso patebulo la ziwanda.​—1 Akor. 10:21.

Munthu akangomeza chakudya, zinthu zimangochitika zokha moti chakudyacho chimakhala mbali ya thupi lake. Chakudya chabwino chingachititse munthu kukhala wathanzi koma ngati si chabwino chingamudwalitse. Koma nthawi zina zotsatira zake sizionekera msanga. N’chimodzimodzi ndi zosangalatsa. Munthu akhoza kusankha zimene akufuna kusangalala nazo. Koma pambuyo posangalala nazo, zinthu zimangochitika zokha ndipo zimakhudza maganizo ndi mtima wake. Zosangalatsa zabwino zimatitsitsimula koma ngati si zabwino zimatisokoneza. (Yak. 1:14, 15) Ngati sitisankha bwino, mwina zotsatira zake sizingaonekere msanga koma pakapita nthawi zidzaonekera. N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho. Pakuti amene akufesa ndi cholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera m’thupi lakelo.” (Agal. 6:7, 8) Choncho tiyenera kupeweratu zosangalatsa zomwe zimalimbikitsa zinthu zimene Yehova amadana nazo.​—Sal. 97:10. w19.10 30 ¶12-14

Lachitatu, February 17

Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi.​—Aef. 5:1, 2.

Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri pamene anapereka Mwana wake nsembe kuti atiwombole. (Yoh. 3:16)Kodi tingatsanzire bwanji chikondi cha Yehova? Tiyenera kuona kuti Mkhristu aliyense ndi wamtengo wapatali kwambiri. Komanso tiyenera kulandira bwino aliyense amene anali ngati “nkhosa yosochera” yemwe wabwerera kwa Yehova. (Sal. 119:176; Luka 15:7, 10) Timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu tikamachita khama kuti tiwathandize akavutika. (1 Yoh. 3:17) Yesu analamula otsatira ake kuti azisonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. (Yoh. 13:34, 35) Lamulo la Yesuli linali latsopano chifukwa linkafuna kuti anthu azisonyeza chikondi chosiyana ndi chimene ankalamulidwa kusonyeza m’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Tikutero chifukwa chakuti lamuloli linawalamula kukonda anzawo ngati mmene Yesu anawakondera. Izi zikutanthauza kuti ankafunika kusonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Choncho tiyenera kukonda abale ndi alongo athu kuposa mmene timadzikondera tokha. Tiyenera kuwakonda kwambiri mpaka kukhala okonzeka kuwafera ngati mmene Yesu anachitira. w19.05 4 ¶11-13

Lachinayi, February 18

Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.​—Luka 11:9.

Kuti tilandire mzimu woyera, tiyenera kupempha Mulungu mosalekeza. (Luka 11:13) Fanizo la Yesu la pa Luka 11:5-9 likusonyeza chifukwa chimene Yehova angatipatsire mzimu woyera. Munthu wamufanizoli ankafuna kusamalira bwino mlendo wake yemwe anafika usiku. Iye ankafuna kumupatsa chakudya koma analibe kalikonse. Ndiye Yesu ananena kuti mnzakeyo anapereka chakudyacho chifukwa choti munthuyo anakakamira kupempha. Kodi mfundo ya Yesu inali yotani? Ngati munthu yemwe si wangwiro anathandiza mnzake chifukwa choti anakakamira, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wokoma mtima? Iye adzaperekanso mzimu woyera kwa anthu amene amamupempha mosalekeza. Choncho tikamachonderera Yehova kuti atipatse mzimu woyera tisamakayikire kuti adzatipatsa. (Sal. 10:17; 66:19) Tisamakayikire kuti tikhoza kutumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale kuti Satana akuyesetsa kutisokoneza. w19.11 13 ¶17-19

Lachisanu, February 19

Bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.​—Maliko 6:31.

Yesu ankadziwa kuti nthawi zina iye ndi atumwi ankafunika kupuma. Komabe anthu ambiri pa nthawiyo komanso masiku ano ali ngati munthu wachuma wamufanizo la Yesu. Munthuyo anadziuza kuti: “Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.” (Luka 12:19; 2 Tim. 3:4) Iye ankaona kuti chofunika kwambiri ndi kupuma komanso kusangalala. Koma Yesu ndi atumwi ake sankaona kuti kuchita zofuna zawo n’kumene kunali kofunika kwambiri. Tiyenera kutsanzira Yesu pogwiritsa ntchito nthawi yathu yopuma kuti tichitenso zinthu zabwino monga kulalikira ndi kupezeka pamisonkhano. Tiziona kuti kuphunzitsa anthu komanso kupezeka pamisonkhano ndi kofunika kwambiri ndipo tiziyesetsa kuti tisamalephere kuchita zinthuzi. (Aheb. 10:24, 25) Ngakhale titapita kutchuthi, tiziyesetsabe kusonkhana komanso kulalikira anthu amene tingakumane nawo.​—2 Tim. 4:2. w19.12 7 ¶16-17

Loweruka, February 20

Malizitsani kupatsa kumeneku.​—2 Akor. 8:11.

Yehova amatipatsa ufulu wosankha zochita pa moyo wathu ndipo iye amatiphunzitsa kuti tizisankha bwino zochitazo. Komanso tikasankha zinthu zomusangalatsa, amatithandiza kuti tizikwaniritse. (Sal. 119:173) Tikamatsatira kwambiri nzeru zochokera m’Mawu a Mulungu m’pamene timatha kusankha bwino zochita. (Aheb. 5:14) Koma ngakhale titasankha mwanzeru, tikhoza kuvutika kuti timalizitse zimene tinayamba kuchita. Taganizirani zitsanzo izi. M’bale wachinyamata waganiza zoti awerenge Baibulo lonse. Ndiye wayamba kuwerenga kwa milungu ingapo kenako n’kusiya pa zifukwa zina. Mlongo wina akufuna kuyamba upainiya koma akungozengereza. Akulu ena agwirizana kuti azichita kwambiri maulendo aubusa koma miyezi ingapo yadutsa asanayambe. Zitsanzozi ndi zosiyana koma zikufanana pa mfundo imodzi. Onse anasankha zochita koma sanazichite. w19.11 26 ¶1-2

Lamlungu, February 21

Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.​—Miy. 21:5.

Yesu ananena kuti nthawi yathu ikufanana ndi “masiku a Nowa” ndipo n’zosachita kufunsa kuti tikukhala “masiku otsiriza” komanso ‘nthawi yovuta.’ (Mat. 24:37; 2 Tim. 3:1) Chifukwa cha zimenezi, mabanja ena asankha kuti asakhale ndi ana panopa n’cholinga choti azichita zambiri mu utumiki. Anthu anzeru ‘amawerengera’ zimene zingafunike asanasankhe kukhala ndi ana komanso kuchuluka kwa ana amene angakhale nawo. (Luka 14:28, 29) Makolo amavomereza kuti kulera ana kumafuna ndalama zambiri, nthawi ndiponso mphamvu. Choncho anthu ayenera kuganizira mafunso ngati awa: ‘Kodi tonsefe tingafunike kugwira ntchito kuti tizipezera banja lathu zofunika pa moyo? Nanga tonsefe tili ndi maganizo ofanana pa nkhani yoti zofunika pa moyo ndi ziti? Ngati tonsefe tingafunike kugwira ntchito, kodi ndi ndani azidzasamalira ana athu? Nanga tingafune kuti ana athu atengere maganizo ndi zochita za ndani?’ Anthu amene amakambirana mafunsowa modekha amatsatira mfundo ya pa lemba la leroli. w19.12 23-24 ¶6-7

Lolemba, February 22

Okhawa ndiwo antchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa.—Akol. 4:11.

Mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto oopsa motsatizanatsatizana. (2 Akor. 11:23-28) Iye anafunikanso kupirira “munga m’thupi” womwe mwina ukutanthauza vuto linalake la m’thupi mwake. (2 Akor. 12:7) Iye anakhumudwanso pamene mnzake wina dzina lake Dema anamusiya “chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Paulo anali Mkhristu wodzozedwa, wolimba mtima komanso wodzipereka pothandiza ena, koma nthawi zina ankakhumudwa. (Aroma 9:1, 2) Paulo anathandizidwa komanso kulimbikitsidwa. Choyamba, Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti amulimbikitse. (2 Akor. 4:7; Afil. 4:13) Chachiwiri, anagwiritsa ntchito Akhristu ena kuti alimbikitse Paulo. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti Akhristu ena amene ankatumikira nawo ‘anamuthandiza komanso kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:11) Ena mwa anthu amene anawatchula anali Arisitako, Tukiko ndi Maliko. Anthu amenewa analimbikitsa Paulo ndiponso kumuthandiza kuti apirire mavuto ake. w20.01 8 ¶2-3

Lachiwiri, February 23

Maso a mtima wanu aunikiridwa.​—Aef. 1:18.

Yesu anasonyeza kuti n’zovuta kufotokozera munthu amene sanadzozedwe zimene zimachitika munthu ‘akabadwanso’ kapena kuti ‘akabadwa mwa mzimu.’ (Yoh. 3:3-8) Kodi munthu akadzozedwa maganizo ake amasintha bwanji? Yehova asanadzoze munthu, munthuyo amayembekezera ndi mtima wonse kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Amayembekezera kudzaona Mulungu atachotsa zoipa zonse n’kusintha dzikoli kuti likhale lokongola kwambiri. Mwina amayembekezeranso kudzaonana ndi anzake kapena achibale ake amene anamwalira. Koma akadzozedwa, maganizo ake amasinthiratu. Si kuti amangoyamba kuganiza kuti moyo wosatha padziko lapansi sungakhale wosangalatsa. Sasinthanso chifukwa chopanikizika ndi mavuto kapena nkhawa. Si kutinso amangoyamba kuganiza kuti moyo wapadzikoli udzakhala wotopetsa. M’malomwake, Yehova ndi amene amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti asinthe maganizo a munthuyo komanso zimene amayembekezera. w20.01 22 ¶9-11

Lachitatu, February 24

Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.—Aroma 13:1.

Amuna a Chiisiraeliwo ankakhala ndi udindo wosamalira nkhani zokhudza kulambira komanso milandu ina. Koma udindo wa akulu amene amatsatira “chilamulo cha Khristu” ndi wongosamalira nkhani zokhudza kulambira basi. (Agal. 6:2) Iwo amazindikira kuti akuluakulu a boma ndi amene apatsidwa udindo ndi Mulungu kuti azisamalira milandu ina yosakhudza kulambira. Iwo ali ndi udindo wopatsa munthu chilango monga kumulipiritsa kapena kumumanga. (Aroma 13:2-4) Kodi akulu amachita chiyani ngati munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu? Iwo amagwiritsa ntchito Malemba posankha zochita pa nkhani zimenezi. Amakumbukiranso kuti maziko a chilamulo cha Khristu ndi chikondi. Zimenezi zimawachititsa kuganizira funso lakuti: Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tithandize anthu mumpingo amene alakwiridwa? Pothandiza munthu wolakwayo, akulu achikondi amaganizira mafunso akuti: Kodi munthuyu ali ndi mtima wolapa? Nanga kodi tingamuthandize bwanji kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova? w19.05 7 ¶23-24

Lachinayi, February 25

Ine ndili ndi moyo chifukwa cha Atate.​—Yoh. 6:57.

Yesu anatsimikizira mfundo yoti Atate wake ndi amene anamupatsa moyo komanso kumuthandiza kuti akhalebe moyo ponena mawu a mulemba laleroli. Iye ankadalira kwambiri Atate wake ndipo ankamupatsa zofunika pa moyo. Koposa zonse, Yehova ankasamalira Yesu mwauzimu. (Mat. 4:4) Yehova amatipatsanso zinthu zothandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Mawu ake amatiuza zoona zake zokhudza iyeyo, zolinga zake, chifukwa chake anatilenga komanso zimene zidzachitike m’tsogolo. Yehova anasonyeza kuti amatiganizira potithandiza kuti tiphunzire za iye, kaya kuchokera kwa makolo athu kapena anthu ena. Amapitiriza kutithandiza pogwiritsa ntchito akulu komanso abale ndi alongo athu. Iye amatipatsanso malangizo kumisonkhano yampingo komwe amatiphunzitsa limodzi ndi Akhristu anzathu. Kunena zoona, pali njira zambiri zimene Yehova amasonyezera kuti amatikonda.​—Sal. 32:8. w20.02 3 ¶8; 5 ¶13

Lachisanu, February 26

Tiyeni titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.​—Aroma 14:19.

Ngati anthu akuchitirana nsanje, mtendere sungakhalepo. Choncho tiyenera kuchotseratu nsanje mumtima mwathu komanso kupewa zinthu zimene zingayambitse nsanje m’mitima ya anthu ena. Kodi tingathandize bwanji anthu ena kuti asayambe mtima wansanje, nanga tingalimbikitse bwanji mtendere? Zochita zathu zimakhudza kwambiri anthu ena. Dzikoli limalimbikitsa mtima ‘wodzionetsera ndi zinthu zimene tili nazo.’ (1 Yoh. 2:16) Koma mtima umenewu ndi umene umalimbikitsa nsanje. Kuti tithandize ena kupewa nsanje, tiyenera kupewa kulankhulalankhula za zinthu zimene tili nazo kapena zimene tikufuna kugula. Tingachitenso bwino kukhala ndi maganizo odzichepetsa pa nkhani ya maudindo amene tili nawo mumpingo. Tikutero chifukwa chakuti tikamadzionetsera pa maudindo amene tili nawo tingachititse anthu ena kuyamba nsanje. Koma tikamasonyeza kuti timaganizira anthu ena komanso kuwayamikira pa zinthu zabwino zimene amachita, timawathandiza kuti azikhala okhutira ndipo timalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere mumpingo. w20.02 18 ¶15-16

Loweruka, February 27

Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.—Aroma 1:20.

Mukhoza kuphunzira za Yehova poona chilengedwe. (Chiv. 4:11) Mungaone nzeru za Yehova mukaganizira mmene anapangira zomera ndi nyama. Muziganizira njira yodabwitsa imene anapangira thupi lanu. (Sal. 139:14) Muziganiziranso mphamvu zimene Yehova anaika m’dzuwa lomwe ndi imodzi mwa nyenyezi mabiliyoni ambiri. (Yes. 40:26) Mukatero mudzayamba kulemekeza kwambiri Yehova. Koma kungodziwa kuti Yehova ndi wanzeru komanso wamphamvu ndi chiyambi chabe choti akhale mnzanu. Muyenera kudziwa zambiri zokhudza iyeyo kuti mukhale naye pa ubwenzi wolimba. Muyenera kutsimikizira kuti Yehova amakukondani inuyo panokha. Kodi inuyo zimakuvutani kukhulupirira kuti amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi amakudziwani komanso kukukondani? ‘Tikamufunafuna adzalola kuti timupeze.’ (1 Mbiri 28:9) Ndipotu Yehova wakukokani kuti mumuyandikire. (Yer. 31:3) Munthu akazindikira zinthu zambiri zimene Yehova wamuchitira m’pamene amayamba kumukonda kwambiri. w20.03 4 ¶6-7

Lamlungu, February 28

Popeza tili ndi utumiki umenewu malinga ndi chifundo chimene tinasonyezedwa, sitikubwerera m’mbuyo.​—2 Akor. 4:1.

Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino poika utumiki pamalo oyamba. Pamene anafika ku Korinto pa ulendo wake wachiwiri waumishonale, ndalama zinamuthera ndipo anafunika kugwira ntchito yokonza matenti. Koma si kuti iye ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri. Iye ankagwira ntchitoyi n’cholinga choti azipeza zofunika uku akuchita utumiki. Paulo sankafuna kuti Akhristu a ku Korinto ataye ndalama zawo pomusamalira. (2 Akor. 11:7) Ngakhale kuti Paulo ankafunika kugwira ntchito ina, iye ankaonabe kuti utumiki ndi wofunika kwambiri moti ankalalikira pa tsiku la Sabata lililonse. Zinthu zitasintha pa moyo wake, Paulo anatha kuchita zambiri mu utumiki kuposa kale. Iye “anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu. Iye anali kuchitira umboni kwa Ayuda ndi kuwatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.” (Mac. 18:3-5; 2 Akor. 11:9) Patapita nthawi, Paulo anamangidwa ku Roma kwa zaka ziwiri, koma ankalalikira anthu amene ankabwera kudzamuona komanso ankalemba makalata. (Mac. 28:16, 30, 31) Paulo ankaonetsetsa kuti china chilichonse chisasokoneze utumiki wake. w19.04 4 ¶9

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena