March
Lolemba, March 1
“Lekanani nawo,” watero Yehova. “Musakhudze chinthu chodetsedwa.”—2 Akor. 6:17.
Kukonda Mulungu ndi Mawu ake kumatilimbikitsa kumvera Yehova ngakhale pa nthawi imene achibale kapena anzathu akutikakamiza kuti tichite miyambo yokhudza anthu akufa. Mwina angatinyoze potinena kuti sitikonda kapena kulemekeza anthu amene amwalirawo. Mwinanso anganene kuti zochita zathu zingachititse kuti anthu akufawo avulaze anthu ena amoyo. Ku Caribbean, anthu amakhulupirira kuti munthu akamwalira, mzimu wake umakhala m’deralo ndipo umalanga anthu onse amene ankamuchitira zoipa. Ena amanena kuti mzimuwo ukhoza kubweretsa mavuto m’dera lonse. M’mayiko ena a ku Africa, anthu amasonkha moto usiku wonse panyumba imene pali maliro. Ena amati zimenezi zimathandiza kuti mizimu yoipa isabwere panyumbapo. Koma anthu a Yehovafe sitichita nawo miyambo kapena kukhulupirira zinthu zimene zinayamba chifukwa cha mabodza a Satana.—1 Akor. 10:21, 22. w19.04 16 ¶11-12
Lachiwiri, March 2
Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.—Mat. 7:12.
Yesu ankaphunzitsa mfundo zimene zinkathandiza otsatira ake kuti azichita zinthu mwachilungamo. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo ya m’lemba lathu la lero. Tonsefe timafuna kuti anthu azitichitira zinthu mwachilungamo. Choncho nafenso tiyenera kuwachitira zinthu mwachilungamo. Tikatero, nawonso akhoza kutichitira zomwezo. Koma kodi tingatani ngati tachitiridwa zinthu mopanda chilungamo? Yesu anaphunzitsanso kuti tisamakayikire kuti Yehova ‘adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku.’ (Luka 18:6, 7) Tingati mawu amenewa akulonjeza kuti: Mulungu wathu wachilungamo amadziwa mavuto amene tikukumana nawo m’masiku otsirizawa ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nthawi yoyenera. (2 Ates. 1:6) Tikamatsatira mfundo zimene Yesu anaphunzitsa tidzayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Komanso ngati tachitiridwa zinthu mopanda chilungamo m’dziko la Satanali, tizikumbukira kuti Yehova adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. w19.05 5 ¶18-19
Lachitatu, March 3
Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.—1 Pet. 3:15.
Kodi ndinu wachinyamata ndipo muli pasukulu? Anzanu onse akhoza kumakhulupirira kuti kuimba nawo nyimbo ya fuko n’kofunika. Ndiyeno inuyo mumafuna kuwafotokozera zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi koma mumadzikayikira. Zikatero chofunika kuchita n’kuifufuza nkhaniyi. Pofufuzapo mungakhale ndi zolinga ziwiri. Choyamba, mungafune kutsimikizira panokha kuti sitiyenera kukhala mbali ya dziko. Chachiwiri, mungafune kupeza njira yabwino yofotokozera zimene mumakhulupirirazo. (Yoh. 17:16) Mwina mungayambe ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi anzanga angapereke zifukwa ziti zosonyeza kuti tiyenera kuimba nyimbo ya fuko?’ Kenako mungafufuze nkhaniyi m’mabuku athu. Mukatero mudzaona kuti kufotokoza zimene mumakhulupirira si kovuta ngati mmene munkaganizira. Anthu ambiri amaganiza kuti ayenera kuimba nawo nyimboyi chifukwa choti munthu wina amene amamulemekeza anawauza kuti aziimba. Mukangopeza mfundo imodzi kapena ziwiri mukhoza kukayankha bwinobwino munthu amene akufunadi kudziwa zoona pa nkhaniyi.—Akol. 4:6. w19.05 29 ¶13
Lachinayi, March 4
Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.—Yes. 66:13.
Pamene Eliya ankathawa, anavutika kwambiri maganizo moti ankaona kuti bola kungofa. Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo kwa mneneriyu ndipo mngeloyo anachita zinthu zomuthandiza. Iye anapatsa Eliya chakudya chotentha bwino n’kumuuza kuti adye. (1 Maf. 19:5-8) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Nthawi zina, kungochita zinthu zochepa kungathandize kwambiri munthu. M’bale kapena mlongo amene akuvutika maganizo akhoza kulimbikitsidwa kwambiri ngati titangomuchitira zinthu monga kumukonzera chakudya, kumupatsa kamphatso kapena kumulembera kakhadi. Ngati timavutika kukambirana ndi anthu nkhani yachinsinsi kapena imene ikuwapweteka kwambiri, tikhoza kuchita zinthu zothandiza ngati zimenezi. Yehova anamupatsa Eliya mphamvu zodabwitsa kuti athe kuyenda mtunda wautali mpaka kukafika kuphiri la Horebe, komwe adani ake sangamupezenso. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Ngati tikufuna kulimbikitsa anthu amene anachitiridwa nkhanza, choyamba tiyenera kuwathandiza kuzindikira kuti ndi otetezeka, kaya kunyumba kwawo kapena ku Nyumba ya Ufumu. w19.05 16 ¶11; 17 ¶13-14
Lachisanu, March 5
Anthu a m’dziko lonselo adzalira mokuwa. . . . Banja la nyumba ya Natani lizidzalira palokha.—Zek. 12:12.
Tiyerekeze kuti mukuwerenga chaputala 12 m’buku la Zekariya chomwe chinalosera za imfa ya Mesiya. (Zek. 12:10) Mutafika pavesi 12 mukuwerenga kuti “banja la nyumba ya Natani” lidzalira kwambiri Mesiya akadzaphedwa. Ndiye m’malo mongopitiriza kuwerenga, mukudzifunsa kuti, ‘Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa banja la Natani ndi Mesiya?’ Pofuna kupeza yankho la funsoli, mukuyamba kufufuza. Mukupeza kuti pavesili pali lifalensi ya 2 Samueli 5:14 ndipo ikunena kuti Natani anali mwana wa Mfumu Davide. Lifalensi ina ndi ya Luka 3:31 ndipo ikusonyeza kuti Yesu anali mbadwa ya Natani kudzera mwa Mariya. Ndiyeno mwayamba kuchita chidwi kwambiri. Munkadziwa kuti Baibulo linaneneratu kuti Yesu adzakhala mwana wa Davide. (Mat. 22:42) Koma Davide anali ndi ana aamuna oposa 20. Choncho n’zodabwitsa kuti Zekariya ananeneratu kuti banja la Natani ndi limene lidzalira kwambiri chifukwa cha imfa ya Yesu. w19.05 30 ¶17
Loweruka, March 6
Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.—Aroma 12:2.
Kodi tiyenera kuchita chiyani? Tikamaphunzira mwakhama tikhoza kutsimikizira kuti mfundo zimene timaphunzira m’Baibulo n’zoona. Izi zingathandize kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti mfundo za Yehova ndi zachilungamo. Mofanana ndi mtengo umene uli ndi mizu yolimba, tikhoza ‘kukhazikika m’chikhulupiriro.’ (Akol. 2:6, 7) Tisaiwale kuti munthu wina sangatilimbitsire chikhulupiriro chathu. Choncho tiyenera kupitiriza kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu. Tizipemphera pafupipafupi n’kumachonderera Yehova kuti atipatse mzimu wake. Tiziganizira mozama zimene zili mumtima ndi m’maganizo athu. Tizicheza ndi anthu amene angatithandize kuti tisinthe maganizo athu n’kukhala abwino. Tikamatero tidzachotsa maganizo olakwika alionse amene tatengera m’dziko la Satanali. Tidzakwanitsa kugubuduza “maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu.”—2 Akor. 10:5. w19.06 13 ¶17-18
Lamlungu, March 7
Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo.—Yak. 1:27.
Tiyenera kupitiriza kuthandiza anthu amene aferedwa ngati mmene Rute ankathandizira Naomi. (Rute 1:16, 17) Mlongo wina dzina lake Paula anati: “Mwamuna wanga atangomwalira, anthu ankandithandiza kwambiri. Kenako patapita nthawi, anayambanso kutanganidwa ndi zinthu zawo. Koma moyo wanga unali utasinthiratu. Zimakhala bwino kwambiri anthu akazindikira kuti munthu woferedwa amafuna kuthandizidwa kwa miyezi kapenanso zaka.” N’zoona kuti anthu amasiyana ndipo amamva chisoni mosiyananso. Ena amavomereza msanga zimene zawachitikira. Pomwe ena amavutika kwambiri nthawi iliyonse imene akuchita zinthu zimene kale ankachitira limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wawo. Chofunika ndi kukumbukira kuti Yehova watipatsa mwayi komanso udindo wothandiza anthu amene aferedwa mwamuna kapena mkazi wawo. w19.06 24 ¶16
Lolemba, March 8
Ndidzamanga pakamwa panga kuti patetezeke, nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.—Sal. 39:1.
Pamene ntchito yathu yaletsedwa, tiyenera kuzindikira nthawi yoti ‘tikhale chete.’ (Mlal. 3:7) Sitiyenera kuulula zinthu zachinsinsi monga mayina a abale ndi alongo athu, malo amene timasonkhana, mmene timalalikirira ndiponso njira zolandirira chakudya chauzimu. Sitiyenera kuuza akuluakulu a boma zinthu ngati zimenezi kapena kuuza anzathu komanso achibale athu, kaya a m’dziko lathu kapena m’mayiko ena. Zili choncho chifukwa tikawauza tikhoza kuika moyo wa abale athu pa ngozi. Tizipewa kukwiyirana pa nkhani zing’onozing’ono. Satana amadziwa kuti nyumba yogawanika singakhale. (Maliko 3:24, 25) Choncho angamayesetse kuti atigawanitse. Iye amafuna kuti tizilimbana tokhatokha m’malo molimbana ndi iyeyo. Ngakhale Akhristu olimba mwauzimu ayenera kusamala. Tikamayesetsa kuthetsa mavuto mwamsanga sitidzalola kuti chilichonse chitisiyanitse ndi abale athu.—Akol. 3:13, 14. w19.07 11-12 ¶14-16
Lachiwiri, March 9
Kapolo wa Ambuye . . . ayenera kukhala wodekha kwa onse. Ayeneranso kukhala woyenerera kuphunzitsa.—2 Tim. 2:24.
Nthawi zambiri anthu amamvetsera uthenga wathu chifukwa cha mmene timawalankhulira osati chifukwa cha zimene timanena. Anthuwo amayamikira tikamawalankhula mokoma mtima, mwaulemu komanso mowaganizira. Sitiyenera kukakamiza anthu kuti azitimvetsera. Koma tiziyesetsa kumvetsa maganizo awo pa nkhani ya zipembedzo ndiponso kuwalemekeza. Mwachitsanzo, Paulo akamalankhula ndi Ayuda ankagwiritsa ntchito Malemba. Koma polankhula ndi akatswiri a nzeru za Chigiriki ku Areopagi, sanatchule za Baibulo. (Mac. 17:2, 3, 22-31) Kodi tingamutsanzire bwanji? Tikakumana ndi munthu amene sakhulupirira Baibulo, tikhoza kukambirana naye popanda kutchula za Baibulolo. Mukaona kuti munthu wina angachite manyazi anthu ena akamuona akuwerenga nanu Baibulo, mungamusonyeze malemba m’njira yosaonekera, mwina pogwiritsa ntchito chipangizo. w19.07 21 ¶5-6
Lachitatu, March 10
Samalani kuti mitima yanu isakopeke ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiweramira.—Deut. 11:16.
Satana anachita zinthu mochenjera pokopa Aisiraeli kuti ayambe kulambira mafano. Iye ankadziwa kuti Aisiraeliwo ankafunikira chakudya ndipo anagwiritsa ntchito zimenezi kuti awakope. Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa anafunika kusintha njira zawo zaulimi. Ali ku Iguputo, iwo ankathirira mbewu zawo ndi madzi ochokera mumtsinje wa Nailo. Koma m’Dziko Lolonjezedwa anthu sankathirira mbewu. Iwo ankadalira mvula komanso mame. (Deut. 11:10-15; Yes. 18:4, 5) Choncho Aisiraeli ankafunika kuphunzira njira zatsopano zaulimi. N’chifukwa chiyani Yehova anachenjeza Aisiraeli kuti asayambe kulambira milungu yonyenga pamene ankalankhula nawo za ulimi? Iye ankadziwa kuti Aisiraeli angafune kuphunzira njira zaulimi kwa anthu osalambira Mulungu omwe ankakhala nawo pafupi. Ndipo ankadziwa kuti alimi a ku Kananiwo anali atasokonezedwa ndi kulambira Baala.—Num. 25:3, 5; Ower. 2:13; 1 Maf. 18:18. w19.06 3 ¶4-6
Lachinayi, March 11
Ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirire kukula.—Afil. 1:9.
Mtumwi Paulo, Sila, Luka ndi Timoteyo atafika ku Filipi, anapeza anthu ambiri amene ankamvetsera uthenga wa Ufumu. Abale 4 akhamawa anathandiza kukhazikitsa mpingo ndipo abale ndi alongo amumpingo watsopanowu anayamba kusonkhana, mwina kunyumba ya wokhulupirira wina dzina lake Lidiya. (Mac. 16:40) Koma kenako abale ndi alongowa anayamba kukumana ndi mavuto. Satana anachititsa kuti adani ena a choonadi ayambe kutsutsa kwambiri ntchito yolalikira ya Akhristu okhulupirikawa. Paulo ndi Sila anagwidwa, kumenyedwa ndi ndodo komanso kuikidwa m’ndende. Atamasulidwa, anapita kukaona ophunzira atsopanowo n’kuwalimbikitsa. Kenako Paulo, Sila ndi Timoteyo anachoka mumzindawu koma zikuoneka kuti Luka anatsala. Ndiye kodi abale ndi alongo atsopanowo anatani? Mzimu wa Yehova unawathandiza kuti apitirize kumutumikira mwakhama. (Afil. 2:12) Ndipo Paulo ayenera kuti ankawanyadira kwambiri. w19.08 8 ¶1-2
Lachisanu, March 12
Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.—Miy. 22:7.
Kodi inuyo mwasamukapo posachedwapa? Kusamuka kumafuna ndalama ndipo kupanda kusamala mukhoza kutenga ngongole zambiri. Kuti mupewe zimenezi, musamakonde kugula zinthu zosafunika kwenikweni pa ngongole. (Miy. 22:3) Tikapanikizika mwina posamalira wachibale amene akudwala, zingativute kusankha bwino kuchuluka kwa ndalama zimene tiyenera kukongola. Pa nthawi ngati imeneyi, muyenera kupemphera komanso kuchonderera Mulungu kuti akuthandizeni kusankha zochita mwanzeru. Mukatero, Yehova adzayankha mapemphero anu pokupatsani mtendere umene “udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu” kuti musachite zinthu mopupuluma. (Afil. 4:6, 7; 1 Pet. 5:7) Muzigwirizana ndi anthu abwino. Muzifotokoza zimene zili mumtima mwanu kwa anzanu abwino, makamaka anthu amene anakumanapo ndi zimene mukukumana nazo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti maganizo anu akhale m’malo. (Mlal. 4:9, 10) Anzanu amene munapeza kumene munali adzakhalabe anzanu. w19.08 22 ¶9-10
Loweruka, March 13
Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene . . . amatchedwa Haramagedo.—Chiv. 16:16.
N’chifukwa chiyani Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti Megido pofotokoza za nkhondo yaikulu yomaliza? Ku Megido komanso chigwa cha Yezereeli kunkamenyedwa nkhondo zambiri. Ndipo nthawi zina Yehova ankathandiza athu ake pomenya nkhondozo. Mwachitsanzo, “pafupi ndi madzi a ku Megido,” Mulungu anathandiza Baraki, yemwe anali woweruza wa Aisiraeli, kuti agonjetse asilikali a ku Kanani omwe ankatsogoleredwa ndi Sisera. Baraki limodzi ndi mneneri wamkazi dzina lake Debora anathokoza Yehova chifukwa chowapulumutsa modabwitsa. Iwo anaimba kuti: “Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba, zinamenyana ndi Sisera . . . Adani anu onse afafanizidwe chimodzimodzi, ndipo okukondani inu akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalira.” (Ower. 5:19-21, 31) Pa nkhondo ya Aramagedo, adani a Mulungu adzawonongedwanso ndipo anthu onse amene amakonda Mulungu adzapulumuka. Koma nkhondo ziwirizi zimasiyana pa mfundo imodzi yofunika. Pa Aramagedo, anthu a Mulungu sadzamenya nawo nkhondo ndipo sadzakhalanso ndi zida zankhondo. Koma adzakhala ‘amphamvu akadzakhala osatekeseka n’kumakhulupirira’ Yehova ndi gulu lake lankhondo lakumwamba.—Yes. 30:15; Chiv. 19:11-15. w19.09 9 ¶4-5
Lamlungu, March 14
Bwerani kwa ine.—Mat. 11:28.
Njira imodzi imene ingatithandize kuti tipite kwa Yesu ndi kuyesetsa kuphunzira zimene anachita komanso kunena. (Luka 1:1-4) Ndi udindo wathu kuphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu ndipo palibe amene angatichitire zimenezi. Timapitanso kwa Yesu ngati tasankha kubatizidwa n’kukhala wotsatira wake. Njira ina imene ingatithandize kuti tipite kwa Yesu ndi kupempha akulu kuti azitithandiza tikakumana ndi mavuto. Akulu ndi “mphatso za amuna” zimene Yesu amagwiritsa ntchito posamalira nkhosa zake. (Aef. 4:7, 8, 11; Yoh. 21:16; 1 Pet. 5:1-3) Choncho ifeyo tiyenera kupempha akulu kuti azitithandiza. Tisamayembekezere kuti akulu akhoza kudziwa okha zimene tikuganiza kapena tikufunikira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Julian. Iye anati: “Ndinapempha kuti akulu andithandize ndipo ulendo waubusa umene anachita unali ngati mphatso yabwino kwambiri kuposa zonse zimene ndinalandirapo.” Akulu okhulupirika ngati amene anathandiza Julian angatithandize kudziwa “maganizo a Khristu.” Apa tikutanthauza kuti angatithandize kumvetsa bwino mmene Yesu amaganizira ndiponso kutengera chitsanzo chake. (1 Akor. 2:16; 1 Pet. 2:21) Imeneyi ndi mphatso yabwino kwambiri yomwe angatipatse. w19.09 21 ¶4-5
Lolemba, March 15
Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili.—Yoh. 10:16.
Malemba amafotokoza za amuna ndi akazi okhulupirika ambiri amene ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera koma sanali m’gulu la 144,000. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yohane M’batizi. (Mat. 11:11) Chitsanzo china ndi Davide. (Mac. 2:34) Iwo limodzi ndi anthu ena ambirimbiri adzaukitsidwa kuti akhale padziko lapansi. Onsewa limodzi ndi a khamu lalikulu adzapatsidwa mwayi wosonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova komanso ulamuliro wake. Aka n’koyamba kuti Mulungu agwirizanitse anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu yonse. Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kukhala padzikoli, tiyenera kuthandiza anthu onse amene tingathe kuti akhale m’gulu la khamu lalikulu la “nkhosa zina.” Posachedwapa, chisautso chachikulu chidzayamba ndipo Yehova adzawononga maboma komanso zipembedzo zomwe zakhala zikuzunza anthu. A khamu lalikulu akuyembekezera mwayi waukulu kwambiri wodzatumikira Yehova padziko lapansi mpaka kalekale.—Chiv. 7:14. w19.09 31 ¶18-19
Lachiwiri, March 16
M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola.—2 Pet. 3:3.
Pamene dziko la Satanali latsala pang’ono kuwonongedwa, tingayesedwe pa nkhani yokhala okhulupirika kwa Mulungu komanso Ufumu wake. Anthu am’dzikoli akhozanso kupitiriza kutinyoza. Izi zikhoza kuchitika makamaka chifukwa chakuti sitikhala mbali ya dziko. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tikhale okhulupirika panopa kuti tidzathe kukhalabe okhulupirika pa nthawi ya chisautso chachikulu. Pa nthawi ya chisautso chachikulu, abale amene amatsogolera zinthu padzikoli adzasintha. Pa nthawi inayake, odzozedwa onse adzapita kumwamba kuti akamenye nawo nkhondo ya Aramagedo. (Mat. 24:31; Chiv. 2:26, 27) Choncho abale a m’Bungwe Lolamulira sadzakhalanso nafe padzikoli. Koma a khamu lalikulu adzapitiriza kuchita zinthu mwadongosolo. Ndipo abale ena oyenerera a m’khamu lalikululi ndi amene azidzatsogolera zinthu. Tidzayenera kusonyeza kuti ndife okhulupirika pochita zinthu mogwirizana ndi abalewa komanso pomvera malangizo awo ochokera kwa Mulungu. Izi n’zimene zidzathandize kuti tipulumuke. w19.10 17 ¶13-14
Lachitatu, March 17
Kumene inu mupite inenso ndipita komweko . . . Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko.—Rute 1:16, 17.
Naomi ankakonda Yehova komanso kumutumikira mokhulupirika. Koma mwamuna wake ndi ana ake awiri atamwalira ankafuna kusintha dzina lake kuti likhale “Mara,” kutanthauza kuti “Kuwawa.” (Rute 1:3, 5, 20, mawu am’munsi, 21) Pa nthawi imeneyi, mpongozi wake dzina lake Rute sanamusiye koma ankamuthandiza ndiponso kumulimbikitsa. Iye ankalankhula mawu osavuta kumva komanso ochokera mumtima osonyeza kuti ankakonda Naomi. Mwamuna kapena mkazi wa Mkhristu mnzathu akamwalira, Mkhristuyo amafunika kuthandizidwa. Anthu okwatirana amafanana ndi mitengo imene yakulira limodzi. Pakapita zaka, mizu yake imalukanalukana. Ndiyeno mtengo umodzi ukazulidwa n’kufa, mtengo winawo umavutika. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene waferedwa mwamuna kapena mkazi wake. Iye akhoza kumva chisoni kwa nthawi yaitali. w19.06 23 ¶12-13
Lachinayi, March 18
Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.—Yak. 1:14.
Tiyenera kusamala osati pongosankha mtundu wa zosangalatsa komanso kuchuluka kwa nthawi imene timachitira zosangalatsazo. Kupanda kutero, tikhoza kumawononga nthawi yambiri podzisangalatsa tokha osati potumikira Yehova. Choyamba, mungachite bwino kudziwa nthawi imene mumagwiritsa ntchito pochita zosangalatsazo. Mukhoza kulemba nthawi imene mumachita zimenezi pa mlungu umodzi. Mwachitsanzo, mungalembe nthawi imene mumaonera TV, kufufuza zinthu pa intaneti kapena kusewera magemu pafoni yanu. Mukapeza kuti mukugwiritsa ntchito nthawi yambiri mungachite bwino kulemba ndandanda. Pandandandayo, mulembe kaye nthawi imene muzichita zinthu zofunika kwambiri, kenako n’kulemba nthawi imene mungamachite zosangalatsa. Mukatero, mupemphe Yehova kuti azikuthandizani kutsatira ndandanda yanuyo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikhala ndi nthawi komanso mphamvu zokwanira zophunzirira Baibulo, kuchita kulambira kwa pa banja, kupita kumisonkhano komanso kulalikira ndi kuphunzitsa anthu. Zingakuthandizeninso kuti musamadziimbe mlandu chifukwa chowononga nthawi yambiri pa zosangalatsa. w19.10 30 ¶14, 16; 31 ¶17
Lachisanu, March 19
Ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.—Aroma 7:18.
Cha m’ma 55 C.E., Akhristu a ku Korinto anasankha kuchita zinthu zofunika kwambiri. Iwo atamva kuti abale awo a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya akusowa zinthu zofunika, anasankha kuti awathandize. (1 Akor. 16:1; 2 Akor. 8:6) Koma patapita miyezi ingapo, mtumwi Paulo anamva kuti Akhristuwo sanachite zomwe anasankhazo. Izi zikanachititsa kuti mphatso zawo zisatumizidwe ku Yerusalemu pamodzi ndi zimene mipingo ina inapereka. (2 Akor. 9:4, 5) Akhristu a ku Korinto anasankha kuchita zinthu zabwino ndipo Paulo anawayamikira chifukwa cha chikhulupiriro chawo komanso mtima wawo wopatsa. Koma iye ankafunikanso kuwalimbikitsa kuti amalize zimene anayamba kuchitazo. (2 Akor. 8:7, 10, 11) Zimene zinawachitikirazi zikutiphunzitsa kuti ngakhale Akhristu okhulupirika angavutike kukwaniritsa zinthu zabwino zimene anasankha. Izi zingachitike chifukwa si ife angwiro ndipo nthawi zina timazengereza kuchita zinthu. Mwinanso pangachitike zinthu zina zosayembekezereka zomwe zingatilepheretse kukwaniritsa zomwe tinasankha kuchita.—Mlal. 9:11. w19.11 26-27 ¶3-5
Loweruka, March 20
Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro.—Aef. 6:16.
Mofanana ndi chishango chimene chimateteza mbali yaikulu ya thupi, chikhulupiriro chimakutetezani kuti mupewe chiwerewere, chiwawa komanso zinthu zina zoipa zam’dzikoli. Akhristufe tili pa nkhondo yauzimu ndipo adani athu ena ndi mizimu yoipa. (Aef. 6:10-12) Ndiye kodi mungatsimikizire bwanji kuti mwakonzeka kukumana ndi mayesero? Choyamba, muyenera kupempha Mulungu kuti azikuthandizani. Kenako muyenera kuwerenga Baibulo kuti muzidziona mmene Mulungu amakuonerani. (Aheb. 4:12) Paja Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.” (Miy. 3:5, 6) Mogwirizana ndi mfundoyi, mungachite bwino kuganizira zimene mwasankha posachedwapa pa nkhani zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kodi mwakumana ndi vuto lalikulu lazachuma? Kodi munakumbukira lonjezo la Yehova la pa Aheberi 13:5 lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono”? Nanga lonjezoli linakutsimikizirani kuti Yehova akuthandizani? Ngati zili choncho, ndiye kuti mukusamalira bwino chishango chanu chachikhulupiriro. w19.11 14 ¶1, 4
Lamlungu, March 21
Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova. Chipatso cha mimba ndicho mphoto.—Sal. 127:3.
Kuti mwana akule bwino, kholo lililonse limafunika kugwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zambiri pomusamalira. Choncho ngati makolo angabereke ana ambiri motsatizana, angavutike kusamalira mwana aliyense mokwanira. Mabanja amene anabereka ana ambiri motsatizana anavomereza kuti ankapanikizika. Mayi akhoza kutopa kwambiri ndipo izi zingachititse kuti asamakwanitse kuphunzira, kupemphera ndiponso kulalikira mokwanira. Komanso zingamuvute kuti azimvetsera kumisonkhano. Mwamuna wachikondi amayesetsa kuthandiza mkazi wake kusamalira ana kumisonkhano komanso kunyumba. Mwachitsanzo, akhoza kuthandiza mkazi wake ntchito zapakhomo. Bamboyo ayenera kuonetsetsa kuti akuchita kulambira kwa pabanja m’njira yothandiza banja lonse. Ayeneranso kulowa mu utumiki ndi banja lake pafupipafupi. w19.12 24 ¶8
Lolemba, March 22
Chaka cha 50 ndi Chaka cha Ufulu kwa inu.—Lev. 25:11.
Kodi Chaka cha Ufulu chinkawathandiza bwanji Aisiraeli? Tiyerekeze kuti munthu wina anakongola ndalama zambiri moti anafunika kugulitsa malo ake kuti alipire ngongoleyo. Pa Chaka cha Ufulu, munthuyo ankafunika kubwezeredwa malowo. Zikatero munthuyo ‘ankabwerera kumalo ake,’ ndipo malowo ankakhala cholowa cha ana ake. Nthawi zina, munthu ankafunika kugulitsa mwana wake kapena kudzigulitsa yekha kuti akhale kapolo pofuna kulipira ngongole. Pa Chaka cha Ufulu, kapoloyo ankafunika ‘kubwerera ku banja lake.’ (Lev. 25:10) Choncho palibe amene ankakhala kapolo mpaka kalekale. Yehova ananenanso kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsa ndithu m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako.” (Deut. 15:4) Izitu ndi zosiyana kwambiri ndi zimene zikuchitika masiku ano chifukwa anthu olemera akulemeralemerabe pomwe osauka akusaukirasaukirabe. w19.12 8-9 ¶3-4
Lachiwiri, March 23
Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga.—Miy. 27:11.
Yesu akakumana ndi mayesero, ankapemphera “mofuula komanso akugwetsa misozi.” (Aheb. 5:7) Mapemphero akewa anali ochokera pansi pa mtima ndipo anamuthandiza kuti akhalebe womvera. Yehova ankaona kuti mapemphero a Yesu anali ngati kafungo kabwino ka zofukiza. Zonse zimene Yesu ankachita pa moyo wake zinkasangalatsa Yehova komanso kusonyeza kuti Yehovayo ndi woyenera kulamulira. Tikhoza kutsanzira Yesu tikamayesetsa kumvera Yehova mokhulupirika. Tikakumana ndi mayesero tiyenera kumachonderera Yehova kuti atithandize kukhalabe okhulupirika kwa iye. Timadziwa kuti Yehova sangayankhe mapemphero athu ngati timachita zinthu zosemphana ndi zimene iye amafuna. Koma tikamachita zinthu zimene amasangalala nazo sitikayikira kuti iye amaona kuti mapemphero athu ali ngati zofukiza zonunkhira. Sitikayikiranso kuti kumvera ndi kukhulupirika kwathu kumasangalatsa Atate wathu wakumwamba. w19.11 21-22 ¶7-8
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Luka 19:29-44
Lachitatu, March 24
Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?—Mat. 24:45.
Mu 1919, Yesu anasankha kagulu ka abale odzozedwa kuti kakhale “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kapolo ameneyu amatsogolera pa ntchito yolalikira ndipo amapereka “chakudya pa nthawi yoyenera” kwa otsatira a Khristu. Satana ndi dziko lakeli akhala akuyesetsa kuti asokoneze kapena kulepheretseratu ntchito imene kapoloyu amagwira. Mwachitsanzo, pachitika mavuto monga nkhondo ziwiri zapadziko lonse, kuzunzidwa kwa anthu a Yehova, mavuto azachuma komanso zinthu zopanda chilungamo. Ngakhale zili choncho, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wakhala akuperekabe chakudya chauzimu kwa otsatira a Khristu. Masiku ano, chakudya chauzimuchi ndi chambiri, chaulere ndipo chikupezeka m’zilankhulo zoposa 900. Umenewu ndi umboni wosatsutsika wakuti Mulungu akugwiritsa ntchito kapoloyu. Umboni wina ndi wakuti ntchito yolalikira ikuyenda bwino kwambiri moti uthenga wabwino ukulalikidwa “padziko lonse lapansi.”—Mat. 24:14. w19.11 24 ¶15-16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Luka 19:45-48; Mateyu 21:18, 19; 21:12, 13
Lachinayi, March 25
Anamumvera [Khristu] chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.—Aheb. 5:7.
Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, mkulu wa ansembe ankafunika kufukiza zonunkhira asanapereke nsembe. Zimenezi zinkathandiza kuti Mulungu asangalale naye pamene akupereka nsembezo. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Yesu ali padzikoli, ankafunika kuchita chinthu china chofunika kwambiri kuposa kupulumutsa anthu. Ndipo ankayenera kuchita chinthucho asanapereke moyo wake nsembe. Iye ankafunika kukhala wokhulupirika pa moyo wake n’cholinga choti nsembe yake ikhale yovomerezeka kwa Yehova. Pochita zimenezi, Yesu anasonyeza kuti munthu akamamvera Yehova zinthu zimamuyendera bwino kwambiri. Anasonyezanso kuti Atate wake ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Pa nthawi yonse imene Yesu anakhala padziko lapansi, ankatsatira mfundo za Yehova mokhulupirika. Sanalole kuti mayesero, imfa yopweteka kwambiri kapena chinthu china chilichonse chimulepheretse kusonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira.—Afil. 2:8. w19.11 21 ¶6-7
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Luka 20:1-47
Lachisanu, March 26
Inu mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga.—Luka 22:28.
Pa utumiki wake wonse padzikoli, Yesu ankathandizidwa ndi atumwi omwe analinso anzake apamtima. (Miy. 18:24) Yesu ankayamikira kukhala ndi anzake otere. Pa nthawi yonse ya utumiki wake, azichimwene ake sankamukhulupirira. (Yoh. 7:3-5) Pa nthawi ina, achibale ake ankaganiza kuti wapenga. (Maliko 3:21) Koma usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu ananena mawu amulemba la leroli. N’zoona kuti nthawi zina atumwiwo ankamukhumudwitsa, koma Yesu sankaganizira kwambiri zimenezo. M’malomwake ankaona kuti iwo amamukhulupirira. (Mat. 26:40; Maliko 10:13, 14; Yoh. 6:66-69) Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anawauza kuti: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” (Yoh. 15:15) Yesu ankalimbikitsidwa kwambiri ndi anzakewa. w19.04 11 ¶11-12
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Luka 22:1-6; Maliko 14:1, 2, 10, 11
Tsiku la Chikumbutso
Dzuwa Litalowa
Loweruka, March 27
Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.—Aroma 8:16.
Kodi munthu amadziwa bwanji kuti wasankhidwa kupita kumwamba? Tingapeze yankho la funsoli pa mawu amene mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma omwe anali “oitanidwa kukhala oyera.” Kuwonjezera pa mawu amulemba la tsiku la leroli, iye anawauza kuti: “Simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’” (Aroma 1:7; 8:15) Choncho Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu wake potsimikizira odzozedwa kuti asankhidwa kupita kumwamba. (1 Ates. 2:12) Yehova amathandiza anthu odzozedwa kuti asamakayikire ngakhale pang’ono kuti asankhidwa kupita kumwamba. (1 Yoh. 2:20, 27) Akhristu odzozedwa sadalira anthu ena kuti awatsimikizire zoti adzozedwa. w20.01 22 ¶7-8
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Luka 22:7-13; Maliko 14:12-16 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Luka 22:14-65
Lamlungu, March 28
Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.—Yoh. 15:13.
Chilamulo cha Khristu chili ndi maziko abwino kwambiri omwe ndi chikondi. (Agal. 6:2) Yesu ankachita zinthu zonse chifukwa cha chikondi. Munthu akamamvera anthu chisoni kapena kuwachitira chifundo amasonyeza kuti ndi wachikondi. Yesu ankamvera ena chisoni choncho ankaphunzitsa anthu, kuchiritsa odwala, kudyetsa anjala komanso kuukitsa akufa. (Mat. 14:14; 15:32-38; Maliko 6:34; Luka 7:11-15) Yesu ankaika zofuna za ena pamalo oyamba osati zake. Iye anasonyeza chikondi chachikulu kwambiri pamene anapereka moyo wake chifukwa cha anthufe. Tingatsanzire Yesu tikamaika zofuna za anthu ena pamalo oyamba osati zathu. Tingamutsanzirenso tikamayesetsa kumvera chisoni anthu a m’gawo lathu. Tikamawalalikira ndiponso kuwaphunzitsa chifukwa chowamvera chisoni timakhala kuti tikutsatira chilamulo cha Khristu. w19.05 4 ¶8-10
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Luka 22:66-71
Lolemba, March 29
[Yehova] anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi . . . kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu.—Luka 4:18.
Yesu anamasula anthu ku zinthu zolakwika zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa. Pa nthawiyo, Ayuda ambiri anali pa ukapolo wotsatira miyambo ndi zikhulupiriro zabodza. (Mat. 5:31-37; 15:1-11) Atsogoleri achipembedzowo anali ngati akhungu. Iwo anakana Mesiya komanso zimene ankaphunzitsa choncho anakhalabe mumdima komanso machimo awo sanakhululukidwe. (Yoh. 9:1, 14-16, 35-41) Zinthu zolondola zomwe Yesu ankaphunzitsa komanso chitsanzo chake chabwino, zinathandiza anthu ofatsa kudziwa zimene angachite kuti amasulidwe mwauzimu. (Maliko 1:22; 2:23–3:5) Yesu anamasulanso anthu ku ukapolo wa uchimo umene anatengera kwa Adamu. Chifukwa cha nsembe ya Yesu, Mulungu amatha kukhululukira anthu amene amakhulupirira dipo n’kumachita zinthu zosonyeza chikhulupirirocho.—Aheb. 10:12-18. w19.12 10 ¶8; 11 ¶10-11
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66
Lachiwiri, March 30
Kudzeranso mwa iye, . . . munaikidwa chidindo cha mzimu woyera wolonjezedwawo, umene ndi chikole cha cholowa chathu cham’tsogolo.—Aef. 1:13, 14.
Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake potsimikizira Akhristu onse odzozedwa kuti wawasankha. Apa tingati mzimuwo umakhala “chikole,” kapena kuti lonjezo, powatsimikizira kuti adzalandira moyo wosatha kumwamba osati padzikoli. (2 Akor. 1:21, 22) Kodi munthu akangodzozedwa ndiye kuti basi adzapita kumwamba? Ayi. N’zoona kuti sakayikira zoti anasankhidwa kuti adzapite kumwamba. Koma ayenera kukumbukira malangizo akuti: “Abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha, pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono.” (2 Pet. 1:10) Choncho ngakhale kuti munthu wodzozedwa anaitanidwa kuti apite kumwamba, iye amafunika kukhalabe wokhulupirika kuti adzalandire mphotoyo.—Afil. 3:12-14; Aheb. 3:1; Chiv. 2:10. w20.01 21-22 ¶5-6
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Luka 24:1-12
Lachitatu, March 31
Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.—Miy. 12:18.
Chifukwa chimodzi chimene chinachititsa kuti anzake atatu a Yobu asamuchitire chifundo n’chakuti ankangoona nkhaniyi pamwambamwamba. Izi zinachititsa kuti akhale ndi maganizo olakwika n’kuyamba kumuweruza kuti walakwitsa zinazake. Kodi ifeyo tingapewe bwanji zimene anthuwa anachita? Tizikumbukira kuti munthu akakumana ndi vuto, Yehova yekha ndi amene amadziwa nkhani yonse. Choncho ndi bwino kumvetsera mosamala pamene munthu akufotokoza mavuto ake. M’malo mongomva zimene akunena, tiziyesanso kumva ululu umene ali nawo mumtima mwake. Tikatero m’pamene tingamumvere chisoni kwambiri. Mtima wachifundo ungatithandizenso kuti tizipewa kufalitsa miseche yokhudza mavuto amene anzathu akukumana nawo. M’malo molimbikitsa anthu, munthu wamiseche amachititsa kuti anthu asamagwirizane mumpingo. (Miy. 20:19; Aroma 14:19) Iye akhoza kupweteka munthu amene akukumana kale ndi mavuto. (Aef. 4:31, 32) Choncho ndi bwino kuganizira makhalidwe abwino amene munthu ali nawo komanso zimene tingachite kuti timuthandize pa mavuto ake. w19.06 21-22 ¶8-9