Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es21
  • May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2021
  • Timitu
  • Loweruka, May 1
  • Lamlungu, May 2
  • Lolemba, May 3
  • Lachiwiri, May 4
  • Lachitatu, May 5
  • Lachinayi, May 6
  • Lachisanu, May 7
  • Loweruka, May 8
  • Lamlungu, May 9
  • Lolemba, May 10
  • Lachiwiri, May 11
  • Lachitatu, May 12
  • Lachinayi, May 13
  • Lachisanu, May 14
  • Loweruka, May 15
  • Lamlungu, May 16
  • Lolemba, May 17
  • Lachiwiri, May 18
  • Lachitatu, May 19
  • Lachinayi, May 20
  • Lachisanu, May 21
  • Loweruka, May 22
  • Lamlungu, May 23
  • Lolemba, May 24
  • Lachiwiri, May 25
  • Lachitatu, May 26
  • Lachinayi, May 27
  • Lachisanu, May 28
  • Loweruka, May 29
  • Lamlungu, May 30
  • Lolemba, May 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2021
es21

May

Loweruka, May 1

Adzatilangize zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.​—Ower. 13:8.

Kodi makolo angatani pothandiza ana awo kuti azikonda Yehova? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni ngati mmene Manowa anachitira. Komanso muzipereka chitsanzo chabwino. Zimene mungauze ana anu zimakhala zofunika, koma zochita zanu n’zimene zimakhala zofunika kwambiri. N’zosakayikitsa kuti Yosefe ndi Mariya ankapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana awo, kuphatikizapo Yesu. Yosefe ankagwira ntchito mwakhama kuti azisamalira banja lake. Ndipo ankalimbikitsanso anthu a m’banja lake kuti azikonda zinthu zauzimu. (Deut. 4:9, 10) Iye ankapita ndi banja lake ku Yerusalemu “chaka ndi chaka” kukachita mwambo wa Pasika. (Luka 2:41, 42) Amuna ena a pa nthawiyo mwina ankaona kuti ulendowu unali wotopetsa, wautali komanso wowonongetsa ndalama zambiri. Koma n’zoonekeratu kuti Yosefe ankakonda zinthu zauzimu ndipo anaphunzitsa ana ake kuti azichitanso zomwezo. Nayenso Mariya ankadziwa bwino Malemba. Choncho mawu ndi zochita zake ziyenera kuti zinathandiza ana ake kuti azikonda Malemba. w19.12 24-25 ¶9-12

Lamlungu, May 2

Ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo.​—Aroma 7:14.

Zimene Yehova anachita Adamu atachimwa zimasonyeza kuti amatikonda kwambiri. Adamu atachimwa, anachititsa kuti iyeyo komanso anthu onse odzabadwa asakhalenso m’banja la Mulungu losangalala. (Aroma 5:12) Koma Yehova anachita zinthu zothandiza kwambiri. Yehova anapereka chilango kwa Adamu koma nthawi yomweyo anapereka chiyembekezo kwa ana ake. Iye analonjeza kuti anthu omvera adzabwereranso m’banja lake. (Gen. 3:15; Aroma 8:20, 21) Kuti zimenezi zitheke, Yehova anakonza zoti Mwana wake adzapereke dipo. (Yoh. 3:16) Yehova wasonyeza kuti amatikonda ndipo ndi Atate wabwino kwambiri. Iye amamvetsera mapemphero athu ndipo amatipatsa zinthu zonse zimene timafunikira. Amatiphunzitsa komanso kutithandiza ndipo kutsogoloku watisungira madalitso osaneneka. Timasangalala kwambiri kudziwa kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda. w20.02 6 ¶16-17; 7 ¶20

Lolemba, May 3

Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.​—Sal. 94:19.

Kodi munavutikapo ndi nkhawa? Mwina munadapo nkhawa chifukwa chokhumudwa ndi zimene anthu ena ananena kapena kuchita. Apo ayi, mungamade nkhawa ndi zimene inuyo munanena kapena kuchita. Mwachitsanzo, mwina munalakwitsapo zinazake ndipo mumaona kuti Yehova sangakukhululukireni. Mwinanso mumaganiza kuti popeza mumada nkhawa kwambiri, ndiye kuti mulibe chikhulupiriro chokwanira ndipo si inu munthu wabwino. Taganizirani zitsanzo za anthu ena otchulidwa m’Baibulo. Chitsanzo choyamba ndi Hana, yemwe anadzakhala mayi ake a mneneri Samueli. Iye anali ndi chikhulupiriro cholimba koma ankada nkhawa kwambiri chifukwa chakuti munthu wina wa m’banja lake ankamuchitira nkhanza. (1 Sam. 1:7) Nayenso mtumwi Paulo anali ndi chikhulupiriro cholimba koma ankavutika ndi ‘nkhawa imene ankakhala nayo pa mipingo yonse.’ (2 Akor. 11:28) Chitsanzo china ndi Mfumu Davide yemwe anali ndi chikhulupiriro champhamvu ndipo Yehova ankamukonda kwambiri. (Mac. 13:22) Koma Davide analakwitsa zinthu zina zimene zinachititsa kuti azida nkhawa kwambiri. (Sal. 38:4) Yehova anatonthoza atumiki ake onsewa ndipo anawathandiza kuti apezenso mtendere. w20.02 20 ¶1-2

Lachiwiri, May 4

Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha.​—Mat. 16:24.

Munthu asanabatizidwe amafunika kudzipereka. Pochita zimenezi, munthu amapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima n’kumuuza kuti akupereka moyo wake kuti azimutumikira mpaka kalekale. Munthu akadzipereka kwa Mulungu zimatanthauza kuti ‘wadzikana yekha.’ Izi zikutanthauza kuti munthuyo tsopano ndi wa Yehova ndipo umenewu ndi mwayi waukulu kwambiri. (Aroma 14:8) Munthu amauza Yehova kuti chofunika kwambiri pa moyo wake chidzakhala kumutumikira osati kudzisangalatsa. Choncho tingati kudzipereka ndi lumbiro lofunika kwambiri limene timalonjeza kwa Mulungu. Yehova satikakamiza kuti tilonjeze zimenezi. Koma tikalonjeza amafuna kuti tikwaniritse zimene tanenazo. (Sal. 116:12, 14) Kudzipereka kumachitika munthu ali kwayekha ndipo ndi nkhani ya pakati pa munthuyo ndi Yehova. Koma kubatizidwa kumachitika pamaso pa anthu ambiri, makamaka pamsonkhano wadera kapena wachigawo. Munthu akamabatizidwa amasonyeza anthu ena kuti anadzipereka kale kwa Yehova. Choncho ubatizo umasonyeza kuti munthu amakonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, maganizo ake onse ndi mphamvu zake zonse ndipo akufuna kumutumikira mpaka kalekale.​—Maliko 12:30. w20.03 9 ¶4-5

Lachitatu, May 5

Wina asakunyengeni.​—2 Ates. 2:3.

Satana amachititsa anthu kuti aziona Yehova molakwika. Atumwi atamwalira, anthu ena amene ankati ndi Akhristu anayamba kufalitsa zinthu zabodza. (Mac. 20:29, 30) Ampatukowa anachititsa kuti anthu asadziwe bwinobwino za Mulungu woona. Mwachitsanzo, anasiya kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo, n’kuikamo mayina ngati “Ambuye.” Kuchotsa dzina la Mulungu n’kuika mawu akuti “Ambuye” kunasokoneza anthu chifukwa sankaona kusiyana pakati pa Yehova ndi “ambuye” ena otchulidwa m’Baibulo. (1 Akor. 8:5) Iwo ankagwiritsa ntchito mawu oti “Ambuye” ponena za Yehova komanso Yesu. Choncho anthu sankazindikira kuti pali kusiyana pakati pa Yehova ndi Mwana wake ndipo maudindo awo ndi osiyananso. (Yoh. 17:3) Zimenezi zinachititsa anthu kuti ayambe kuphunzitsa mfundo yosemphana ndi Malemba yakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Zotsatira zake n’zakuti anthu amaganiza kuti Mulungu ndi wosamvetsetseka ndipo n’zosatheka kumudziwa. Ilitu ndi bodza lamkunkhuniza.​—Mac. 17:27. w19.06 5 ¶11

Lachinayi, May 6

Ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.​—2 Tim. 4:5.

Kuwonjezera luso lathu pa ntchito yolalikira kumathandiza kuti tizikwaniritsa utumiki wathu. (Miy. 1:5; 1 Tim. 4:13, 15) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kukhala “antchito anzake” a Yehova. (1 Akor. 3:9) Tikamayesetsa ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti’ komanso kuika utumiki pamalo oyamba, utumiki wathu udzakhala wosangalatsa kwambiri. (Afil. 1:10; Sal. 100:2) Kaya mavuto anu ndi aakulu bwanji, simuyenera kukayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzakupatsani mphamvu kuti mukwaniritse utumiki wanu. (2 Akor. 4:1, 7; 6:4) Tikamachita zonse zimene tingathe potumikira Mulungu, ngakhale zitakhala zochepa, tikhoza ‘kukhala ndi zifukwa zosangalalira.’ (Agal. 6:4) Tikamakwaniritsa utumiki wathu timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso anzathu. Ndipo tikamachita zimenezi ‘tidzadzipulumutsa tokha komanso anthu otimvera.’​—1 Tim. 4:16. w19.04 6 ¶15; 7 ¶17

Lachisanu, May 7

Satana . . . akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.—Chiv. 12:9.

Njira yaikulu imene Satana ndi ziwanda amagwiritsa ntchito popusitsa anthu ndi kukhulupirira mizimu. Anthu amene amakhulupirira mizimu amanena kuti angathe kuchita zinthu zodabwitsa. Mwachitsanzo, ena amanena kuti angathe kudziwa zam’tsogolo pogwiritsa ntchito matsenga kapena kungoona mmene nyenyezi zikuonekera. Ena amachita zinthu zosonyeza kuti amatha kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Pomwe ena amachita zamatsenga ndi ufiti moti amati akhoza kulodza munthu. Kafukufuku amene anachitika m’mayiko 18 a ku Latin America ndi ku Caribbean anasonyeza kuti munthu mmodzi pa anthu atatu alionse amakhulupirira zamatsenga ndi ufiti. Ndipo anthu ambiri amakhulupirira kuti n’zotheka kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Kafukufuku wina anachitika m’mayiko 18 a ku Africa ndipo anasonyeza kuti pa anthu 10 alionse, anthu oposa 5 amachita kapena kuopa zaufiti. Koma kaya ifeyo timakhala kuti, tiyenera kusamala kuti tisayambe kukhulupirira mizimu. w19.04 20-21 ¶3-4

Loweruka, May 8

Muonetsetsenso kuti pasakhale wadama.​—Aheb. 12:16.

Yehova Mulungu amadana ndi chinthu chilichonse choipa. (Sal. 5:4-6) Ndiye mukuganiza kuti amamva bwanji munthu akachita tchimo loipa kwambiri logwirira mwana? Popeza timatsanzira Yehova, a Mboni za Yehovafe timadananso kwambiri ndi kugwirira ana moti nkhani imeneyi ikachitika mumpingo sitiilekerera. (Aroma 12:9) Kugwirira mwana ndi kosemphana kwambiri ndi “chilamulo cha Khristu.” (Agal. 6:2) Zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa m’mawu ndi zochita zake anaphunzitsa chifukwa cha chikondi ndipo zimalimbikitsa chilungamo. Popeza Akhristu amatsatira lamulo limeneli, amathandiza ana kuti azimva kuti ndi otetezeka komanso amakondedwa. Koma munthu amene wagwirira mwana amasonyeza kuti ndi wodzikonda komanso wopanda chilungamo. Amachititsanso mwanayo kumva kuti si wotetezeka komanso sakondedwa. N’zomvetsa chisoni kuti Akhristu oona akhudzidwanso ndi nkhani yogwirira ana. N’chifukwa chiyani zafika pamenepa? Masiku ano, anthu oipa akuchuluka ndipo ena amafuna kulowa mumpingo. (2 Tim. 3:13) Anthu enanso amene anali mumpingo amatengeka ndi zilakolako zoipa moti afika pogwirira ana. w19.05 8 ¶1-3

Lamlungu, May 9

Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.​—Yak. 5:16.

Munthu amene akuda nkhawa kwambiri angaganize kuti si woyenera kulankhula ndi Yehova. Kuti tiwalimbikitse, tikhoza kupemphera nawo ndipo tizitchula dzina lawo m’pempherolo. Popempherapo tinganene mawu osonyeza kuti ifeyo komanso abale ndi alongo mumpingo amakonda kwambiri munthuyo. Tingapemphe Yehova kuti alimbikitse komanso kutonthoza mtumiki wake wamtengo wapataliyo. Mapemphero ngati amenewa angalimbikitse kwambiri munthuyo.Tiyenera kuganiza tisanalankhule. Tikamalankhula tisanaganize, mawu athu akhoza kukhala opweteka. Koma tikamalankhula mokoma mtima, anthu amalimbikitsidwa. (Miy. 12:18) Choncho tizipempha Yehova kuti atithandize kusankha bwino mawu n’cholinga choti tilankhule mokoma mtima komanso molimbikitsa. Tizikumbukira kuti mawu a Yehova omwe ali m’Baibulo ndi amphamvu kuposa mawu ena alionse. (Aheb. 4:12) Tikamalimbikitsa anthu, timawathandiza kuzindikira kuti Yehova amawakonda. Tisamaiwalenso kuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Iye amaona nkhanza zilizonse zimene munthu angachitiridwe. Yehova adzaonetsetsa kuti munthu aliyense amene anachita nkhanza ndipo sanalape alangidwe.​—Num. 14:18. w19.05 18 ¶18; 19 ¶19, 21

Lolemba, May 10

Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.—Akol. 2:8.

Satana amafuna kuti tisiye kukonda Yehova. Pofuna kukwaniritsa cholinga chakechi, amayesetsa kusokoneza maganizo athu kuti tiziyendera zofuna zake. Iye amagwiritsa ntchito zimene timalakalaka pofuna kutikopa kuti tizimumvera. (Akol. 2:4) Kodi n’zotheka kuti Mkhristu apusitsidwe ndi Satana? Inde. Kumbukirani kuti Paulo sanapereke chenjezo la pa Akolose 2:8 kwa anthu osakhulupirira. Koma analipereka kwa Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera. (Akol. 1:2, 5) Ngati Akhristu akalewo akanatha kupusitsidwa, kuli bwanji ifeyo masiku ano? (1 Akor. 10:12) Paja Satana anaponyedwa padziko lapansi ndipo akuyesetsa kusocheretsa atumiki okhulupirika a Mulungu. (Chiv. 12:9, 12, 17) Komanso tikukhala pa nthawi imene anthu oipa ndiponso onyenga ‘akuipiraipirabe.’​—2 Tim. 3:1, 13. w19.06 2 ¶1-2

Lachiwiri, May 11

Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova.—1 Maf. 19:4.

Yezebeli ananena kuti adzapha Eliya ndipo Eliyayo anachita mantha kwambiri moti anathawira ku Beere-seba. Iye anakhumudwa kwambiri mpaka kufika ‘popempha kuti afe.’ N’chifukwa chiyani anamva chonchi? Eliya sanali wangwiro ndipo ‘anali munthu ngati ife tomwe.’ (Yak. 5:17) N’kutheka kuti anafooka chifukwa cha nkhawa komanso kutopa kwambiri. Iye ankaganiza kuti zimene ankachita polimbikitsa kulambira koona sizinaphule kanthu. Ankaonanso kuti palibe chilichonse chimene chasintha mu Isiraeli ndipo mtumiki wa Yehova amene watsala ndi iye yekha. (1 Maf. 18:3, 4, 13; 19:10, 14) Yehova anamvetsa Eliya ndipo sanamukalipire. M’malomwake, anamuthandiza kuti apezenso mphamvu. (1 Maf. 19:5-7) Kenako Yehova anamuthandiza kusintha maganizo ake pomusonyeza mphamvu zake zodabwitsa. Anamuuzanso kuti padakali anthu 7,000 mu Isiraeli amene salambira Baala. (1 Maf. 19:11-18) Apatu Yehova anasonyeza Eliya kuti ankamukonda kwambiri. w19.06 15-16 ¶5-6

Lachitatu, May 12

Muzigonjera amuna achikulire. . . . Muzichitirana zinthu modzichepetsa, chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza.​—1 Pet. 5:5.

Tizitsatira malangizo nthawi zonse. Tikhoza kupewa mavuto ambiri tikamamvera malangizo amene abale audindo odalirika atipatsa. Mwachitsanzo, boma litaletsa ntchito yathu m’dziko lina, abale audindo anapereka malangizo akuti tisamagawire mabuku kapena magazini mu utumiki. Koma m’bale wina amene ankachita upainiya sanamvere ndipo ankagawira zinthu zimenezi. Kodi mukudziwa zimene zinachitika? M’baleyu ndi anzake atangomaliza kulalikira mwamwayi, apolisi anafika n’kuyamba kuwafunsa mafunso. Zikuoneka kuti apolisiwo ankawatsatira pamene ankachita zimenezi ndipo analanda mabuku amene anagawirawo. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ndi bwino kutsatira malangizo ngakhale amene tikuganiza kuti si abwino. Nthawi zonse Yehova amatidalitsa tikamatsatira malangizo ochokera kwa abale amene wawasankha kuti azititsogolera.​—Aheb. 13:7, 17. w19.07 12 ¶17

Lachinayi, May 13

Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.​—2 Tim. 3:12.

Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu ananena kuti anthu onse omutsatira adzadedwa. (Yoh. 17:14) Mpaka pano, Akhristu okhulupirika amazunzidwa ndi anthu amene amadana ndi kulambira koona. Ndipo pamene mapeto akuyandikira, adani athu azititsutsa kwambiri. (Mat. 24:9) Ndiye kodi tingakonzekere bwanji panopa? Si bwino kuyesa kuganizira zinthu zoipa zimene zingatichitikire. Tikutero chifukwa chakuti zikhoza kutichititsa mantha kapena kutidetsa nkhawa kwambiri. Ndiyeno tikhoza kugonjeratu mayesero enieni asanafike. (Miy. 12:25; 17:22) Mantha ndi chida champhamvu chimene ‘mdani wathu Mdyerekezi’ amagwiritsa ntchito pofuna kutisokoneza. (1 Pet. 5:8, 9) Choncho tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova panopa. w19.07 2 ¶1-3

Lachisanu, May 14

Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.​—Mat. 28:19.

Yesu ataukitsidwa anakonza zoti akakumane ndi ophunzira ake m’mbali mwa phiri linalake. (Mat. 28:16) Ophunzira akewo ayenera kuti ankayembekezera mwachidwi kuti amve zimene angawauze. N’kutheka kuti pa nthawiyi m’pamene Yesu ‘anaonekera kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.’ (1 Akor. 15:6) N’chifukwa chiyani Yesu anakonza zoti akumane ndi ophunzira akewo? Iye ankafuna kuwapatsa ntchito yofunika kwambiri, chifukwa anawauza kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:18-20) Ophunzira amene anamva mawu a Yesuwa anadzakhala mumpingo wachikhristu woyambirira. Ntchito yaikulu ya mpingowo inali yothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Khristu. Masiku ano, padzikoli pali mipingo masauzande ambiri ndipo ntchito yake yaikulu ndi yomweyi. w19.07 14 ¶1-2

Loweruka, May 15

Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.​—Mlal. 1:4.

Woyang’anira dera wina wa ku Norway ananena kuti anthu amene sakonda kukambirana za Mulungu nthawi zambiri amalolera kukambirana za mavuto am’dzikoli. Choncho iye akapereka moni kwa anthu, amawafunsa kuti: “Kodi inuyo mumaganiza kuti n’chiyani chingathandize kuti tsogolo lathu likhale labwino? Kodi amene angatithandize ndi andale, asayansi kapena munthu wina?” Akamva maganizo awo, amawerenga kapena kungotchula lemba limene limasonyeza kuti m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwino. Ena amasangalala kumva lonjezo la m’Baibulo lakuti dzikoli silidzatha ndipo anthu abwino adzakhalamo mpaka kalekale. (Sal. 37:29) Tiyenera kusintha njira zolalikirira mogwirizana ndi anthu amene takumana nawo. Tikutero chifukwa chakuti chimene chingasangalatse munthu wina chikhoza kumunyansa wina. Ena sadandaula kungoyamba kukambirana za Mulungu kapena Baibulo, pomwe ena amafuna kuti muyambe kaye n’kukambirana nkhani zina. Kaya zinthu zili bwanji, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tilalikire kwa anthu a mitundu yonse. (Aroma 1:14-16) Yehova ndi amene amakulitsa mbewu za choonadi m’mitima ya anthu oyenerera.​—1 Akor. 3:6, 7. w19.07 22-23 ¶10-11

Lamlungu, May 16

Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda chonchi, ndiye kuti ifenso tiyenera kukondana.—1 Yoh. 4:11.

Chikondi cha Mulungu chimatilimbikitsanso kuti tizikonda abale athu. (1 Yoh. 4:20, 21) Mwina tikhoza kuganiza kuti mwachibadwa tingathe kumakonda abale ndi alongo athu. Paja tonse timalambira Yehova n’kumayesetsa kutsanzira makhalidwe ake. Timatsanziranso Yesu, yemwe amatikonda kwambiri moti analolera kupereka moyo wake chifukwa cha ifeyo. Komatu nthawi zina zikhoza kutivuta kutsatira lamulo loti tizikondana. Eodiya ndi Suntuke anali alongo akhama omwe ‘ankayesetsa kutumikira Mulungu limodzi’ ndi mtumwi Paulo. Koma zikuoneka kuti anasemphana maganizo ndipo anasiya kugwirizana. M’kalata imene Paulo analembera mpingo wawo, iye anatchula Eodiya ndi Suntuke ndipo anawalangiza mosapita m’mbali kuti ayenera kukhala “amaganizo amodzi.” (Afil. 4:2, 3) Paulo anaona kuti ndi bwino kuuzanso mpingo wonse kuti: “Muzichita zinthu zonse popanda kung’ung’udza ndi kutsutsana.”​—Afil. 2:14. w19.08 9 ¶6-7

Lolemba, May 17

Musaleke kunyamulirana zolemetsa.​—Agal. 6:2.

Chosangalatsa n’chakuti mipingo komanso abale ndi alongo ambiri amachita zonse zimene angathe pothandiza anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse kuti asasiye utumiki wawo. Mwachitsanzo, amawalimbikitsa kuti apitirize utumiki, amawapatsa ndalama kapena zinthu zina. Apo ayi, amawathandiza kusamalira achibale awo. Ngati munthu wina amene anali mu utumiki wa nthawi zonse wabwera mumpingo wanu, musamaganize kuti utumiki wake unasintha chifukwa cholephera kapena kulakwitsa chinachake. M’malomwake, muziwathandiza kuti azolowere kusinthako. Muziwalandira bwino komanso kuwayamikira pa zimene achita ngakhale kuti panopa sangachite zambiri chifukwa cha matenda. Muziyesetsa kuti muwadziwe bwino komanso muziphunzira pa zimene achita, zimene akudziwa komanso zimene akumana nazo pa moyo wawo. Poyamba, anthu amene utumiki wawo wasintha angafunike kuwathandiza kuti apeze nyumba, ntchito komanso zinthu zina zofunika. w19.08 23-24 ¶12-13

Lachiwiri, May 18

[Ndidzadziyeretsa] pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.—Ezek. 38:16.

Gogi adzadalira “mphamvu za anthu” kapena kuti mphamvu za asilikali ake. (2 Mbiri 32:8) Koma ifeyo tidzadalira Yehova Mulungu wathu ndipo anthu enawo adzaganiza kuti ndife opusa. Adzaganiza choncho poona kuti milungu ya Babulo Wamkulu sinamuteteze pamene ankawonongedwa ndi “chilombo” komanso ‘nyanga zake 10.’ (Chiv. 17:16) Choncho Gogi adzaganiza kuti sadzavutika kutigonjetsa. Iye adzaukira anthu a Yehova ngati ‘mitambo yophimba dziko.’ Koma Gogi adzazindikira kuti wadziputira tsoka lalikulu. Mofanana ndi Farao pa Nyanja Yofiira, Gogi adzazindikira kuti akulimbana ndi Yehova. (Eks. 14:1-4; Ezek. 38:3, 4, 18, 21-23) Khristu limodzi ndi gulu la angelo ake adzateteza anthu a Mulungu n’kuwonongeratu Gogi ndi asilikali ake. (Chiv. 19:11, 14, 15) Koma kodi Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova komanso amene mabodza ake achititsa mayiko kuti afike pa Aramagedo, zidzamuthera bwanji? Yesu adzatsekera m’phompho Satana ndi ziwanda zake ndipo adzakhala mmenemo kwa zaka 1,000.​—Chiv. 20:1-3. w19.09 11-12 ¶14-15

Lachitatu, May 19

Uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.​—Hab. 2:3.

Anthufe timalakalaka zinthu zabwino zimene Yehova watilonjeza. Koma ngati zimene tikuyembekezera zikuoneka kuti zikuchedwa, tikhoza kufooka. Mwinanso tikhoza kufika potaya mtima. (Miy. 13:12) Izi n’zimene zinachitikira anthu ena kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Pa nthawiyo, Akhristu odzozedwa ambiri ankayembekezera kulandira mphoto yawo kumwamba mu 1914. Koma izi sizinachitike. Kodi anthu okhulupirika anatani ataona kuti zimene ankayembekezera sizikuchitika? Sanafooke chifukwa cholinga chawo chachikulu chinali kutumikira Yehova mokhulupirika osati kulandira mphoto. Iwo ankafunitsitsa kuti athamange pa mpikisano wawo mopirira. N’zosachita kufunsa kuti nanunso mumalakalaka Yehova atayeretsa dzina lake, kusonyeza kuti ndi woyenera kulamulira komanso kukwaniritsa malonjezo ake onse. Dziwani kuti zinthu zimenezi zidzachitika pa nthawi imene Yehova akuona kuti ndi yoyenera. Pamene tikudikira nthawi imeneyo, tiyeni tizitumikira Mulungu mwakhama ndipo tisafooke chifukwa chakuti zinthu zimene tinkayembekezera sizikuchitika. w19.08 4-5 ¶9-10

Lachinayi, May 20

Ndine wofatsa ndi wodzichepetsa.​—Mat. 11:29.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu ena amaona kuti ndine wofatsa komanso wodzichepetsa? Kodi ndimalolera kuchita zinthu zooneka ngati zonyozeka pothandiza ena? Nanga ndimachita zinthu mokoma mtima? Yesu ankagwira ntchito ndi anzake mwamtendere ndipo ankasangalala powaphunzitsa. (Luka 10:1, 19-21) Iye ankalimbikitsa ophunzira ake kuti azifunsa mafunso ndipo ankakonda kumva maganizo awo. (Mat. 16:13-16) Ophunzira ake anali ngati maluwa osamaliridwa bwino. Iwo ankamvetsa bwino zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankabala zipatso kapena kuti ankachita zinthu zabwino. Kodi inuyo mumayang’anira anthu ena? Ngati ndi choncho, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimachita bwanji zinthu ndi ena kuntchito kapena kunyumba? Kodi ndimalimbikitsa mtendere? Nanga ndimalimbikitsa ena kuti azindifunsa mafunso? Kodi ndimakonda kumvetsera maganizo awo?’ Akhristufe sitifuna ngakhale pang’ono kufanana ndi Afarisi omwe sankakonda kufunsidwa mafunso ndipo ankazunza anthu omwe anali ndi maganizo osiyana ndi awo.​—Maliko 3:1-6; Yoh. 9:29-34. w19.09 20 ¶1; 23 ¶9-11

Lachisanu, May 21

Pamene azidzati: “Bata ndi mtendere!” chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.​—1 Ates. 5:3.

Atsogoleri a mayiko nthawi zina amagwiritsa ntchito mawu ngati amenewa polimbikitsa mgwirizano wapadziko lonse. Koma kulengeza za “bata ndi mtendere” kumene Baibulo limafotokoza kudzakhala kosiyana. Tikutero chifukwa chakuti akadzalengeza, anthu ambiri adzaganiza kuti maboma akwanitsadi kubweretsa mtendere ndi chitetezo padziko lonse. Koma zoona zake n’zakuti akadzangolengeza, “chisautso chachikulu” chidzayamba ndipo “chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika.” (Mat. 24:21) Sitikudziwa zimene zidzachititse kuti alengeze komanso mmene angalengezere. Sitikudziwanso ngati adzalengeze maulendo angapo kapena ulendo umodzi wokha. Kaya zidzakhala bwanji, chomwe tikudziwa n’chakuti: Sitiyenera kutengeka nazo n’kumaganiza kuti atsogoleri a mayiko angakwanitsedi kubweretsa mtendere padzikoli. Paja chilengezo chimenechi chidzasonyeza kuti “tsiku la Yehova” latsala pang’ono kwambiri kuti liyambe.​—1 Ates. 5:2. w19.10 8-9 ¶3-4

Loweruka, May 22

Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako . . . adzapulumuka.​—Dan. 12:1.

Nkhondo ya Aramagedo idzakhala chimake cha mapeto a dziko loipali. Koma sitiyenera kuchita mantha chifukwa nkhondoyi ndi ya Mulungu. (Miy. 1:33; Ezek. 38:18-20; Zek. 14:3) Yehova akadzangolamula, Yesu adzatsogolera odzozedwa komanso angelo ambirimbiri pomenya nkhondoyi. Iwo adzamenyana ndi Satana, ziwanda komanso anthu amene ali kumbali ya Satana. (Chiv. 6:2; 17:14) Yehova watilonjeza kuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.” (Yes. 54:17) “Khamu lalikulu” la atumiki a Yehova okhulupirika lidzapulumuka ‘n’kutuluka m’chisautso chachikulu.’ Ndipo lidzapitiriza kuchitira Mulungu utumiki wopatulika. (Chiv. 7:9, 13-17) Kunena zoona, Baibulo limatithandiza kuti tiziyembekezera zam’tsogolo molimba mtima. Sitikayikira kuti “Yehova amateteza okhulupirika.” (Sal. 31:23) Anthu onse amene amamukonda ndiponso kumutamanda adzasangalala kwambiri iye akadzayeretsa dzina lake.​—Ezek. 38:23. w19.10 18-19 ¶17-18

Lamlungu, May 23

Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.​—Miy. 17:17.

Pamene tikuyandikira kwambiri mapeto a “masiku otsiriza,” tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu. (2 Tim. 3:1) Mwachitsanzo, chisankho chitachitika m’dziko lina lakumadzulo kwa Africa, ziwawa zinayambika. Kwa miyezi yoposa 6, abale ndi alongo athu sankatha kuyenda momasuka chifukwa anthu ankamenyana m’dera limene ankakhala. Kodi n’chiyani chinawathandiza pa nthawiyi? Ena anakakhala m’nyumba za abale amene m’dera lawo zinthu zinali bwinoko. M’bale wina ananena kuti: “Pa nthawi yovutayi, ndinayamikira kwambiri kukhala ndi anzanga apamtima chifukwa tinkalimbikitsana.” “Chisautso chachikulu” chikadzayamba, tidzasangalala kwambiri kuti tili ndi anzathu abwino omwe amatikonda. (Chiv. 7:14) Choncho tiyenera kuyamba panopa kupeza anzathu apamtima. (1 Pet. 4:7, 8) Tikutero chifukwa chakuti adani athu azidzayesetsa kusokoneza mgwirizano wathu pogwiritsa ntchito mabodza. Adzayesetsanso kuti tiyambe kudana koma zonse zimene adzachitezi sizidzaphula kanthu. Iwo sadzatha kusokoneza mgwirizano wathu kapena kutilepheretsa kukondana. w19.11 2 ¶1-2; 7 ¶19

Lolemba, May 24

Mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.​—Aef. 6:16.

Satana, yemwe ndi “tate wake wa bodza,” amagwiritsa ntchito anthu ake kuti azifalitsa mabodza okhudza Yehova komanso abale ndi alongo athu. (Yoh. 8:44) Mwachitsanzo, anthu ampatuko amatha kugwiritsa ntchito zinthu monga intaneti kapena TV kuti afalitse mabodza kapena kupotoza mfundo zokhudza gulu la Yehova. Mabodza amenewa ali m’gulu la ‘mivi yoyaka moto’ ya Satana. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu wina akunena mabodza oterewa? Sitiyenera kumvetsera. Tikutero chifukwa choti timakhulupirira Yehova komanso abale athu. Choncho tiyenera kupeweratu ampatuko. Tisalole kuti munthu aliyense kapena chidwi chathu zitichititse kuyamba kukangana ndi ampatuko kapena kulola kuti tiyambe kukhulupirira zimene amanena. Kodi mwakhala mukupewa kumvetsera ampatuko kapena kukangana nawo pa mabodza amene amafalitsa? Ngati ndi choncho, mukuchita bwino kwambiri. Koma tiyenera kukhalabe maso chifukwa Satana angagwiritse ntchito zinthu zinanso pofuna kutisokoneza. w19.11 15 ¶8; 16 ¶11

Lachiwiri, May 25

Yehova amafufuza zolinga [za munthu].​—Miy. 16:2.

Tikamasankha zochita tiyenera kuganizira zifukwa zimene tikusankhira zinazake. Yehova amafuna kuti tizichita zinthu zonse moona mtima. Choncho tiyenera kudzifufuza moona mtima kuti tidziwe zifukwa zimene tikufunira kuchita zinthu zina. Sitiyeneranso kubisira anthu ena zifukwazo. Ngati tasankha zinthu popanda kuzindikira zifukwa zake, tingamavutike kuchita zimene tasankhazo. Mwachitsanzo, m’bale wachinyamata angasankhe kuyamba upainiya wokhazikika. Koma patapita nthawi, angayambe kuvutika kuti akwanitse maola ake ndipo angasiye kusangalala ndi utumikiwu. Mwina ankaganiza kuti akufuna kuyamba upainiya n’cholinga choti azisangalatsa Yehova. Koma kwenikweni ankangofuna kusangalatsa makolo ake kapena munthu wina amene amamulemekeza. Taganizirani chitsanzo china. Tiyerekeze kuti munthu wina amene akuphunzira Baibulo wasankha kuti asiye kusuta. Kwa mlungu umodzi kapena iwiri wayesetsa kwambiri kuti asasute koma kenako walephera kudziletsa ndipo wasutanso. Ndiye patapita nthawi, wakwanitsa kusiyiratu. Iye wakwanitsa chifukwa choti amakonda kwambiri Yehova komanso akufunitsitsa kumusangalatsa.​—Akol. 1:10; 3:23. w19.11 27 ¶9; 29 ¶10

Lachitatu, May 26

Makhalidwe anu akhale oyenera uthenga wabwino wa Khristu.—Afil. 1:27.

Mtumwi Paulo sankakayikira kuti adzakwaniritsa cholinga chake n’kumaliza mpikisano umene ankathamanga. Popeza anali Mkhristu wodzozedwa, ankayembekezera kudzapeza “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba.” Koma ankadziwa kuti ayenera ‘kuyesetsabe’ kuti adzapeze mphotoyo. (Afil. 3:14) Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chochititsa chidwi kuti athandize Afilipi kumvetsa kufunika koyesetsabe kukwaniritsa cholinga chawo. Paulo anakumbutsa Afilipi kuti anali nzika zakumwamba. (Afil. 3:20) N’chifukwa chiyani ankafunika kukumbukira zimenezi? Pa nthawi imeneyo, anthu ankafunitsitsa kukhala nzika ya Chiroma. Koma Akhristu odzozedwa anali nzika za malo abwino kwambiri ndipo akanatha kupeza phindu lalikulu kuposa kukhala nzika ya Chiroma. Akhristu odzozedwa amasiku ano amapereka chitsanzo chabwino akamayesetsabe kuti akapeze mphoto yawo yokakhala ndi moyo wosatha kumwamba. w19.08 6 ¶14-15

Lachinayi, May 27

Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.​—Yoh. 8:36.

Ufulu umenewu ndi waukulu kuposa umene Aisiraeli ankakhala nawo pa Chaka cha Ufulu. (Lev. 25:8-12) Mwachitsanzo, munthu amene anamasulidwa pa chaka chimenechi sakanapewa imfa ndipo akanatha kukhalanso kapolo. Pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova anadzoza ndi mzimu woyera atumwi ndiponso amuna ndi akazi ena okhulupirika. Iye anayamba kuwaona ngati ana ake oti adzalamulire ndi Yesu kumwamba. (Aroma 8:2, 15-17) Iwo anali oyamba kukhala pa ufulu umene Yesu anautchula musunagoge wa ku Nazareti. (Luka 4:16-19, 21) Anthu amenewa anamasulidwa ku ukapolo wotsatira zinthu zabodza zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa komanso makhalidwe awo osemphana ndi Malemba. Mulungu anayambanso kuwaona kuti amasuka ku uchimo ndi imfa. Chaka cha Ufulu chophiphiritsira chimene chinayamba mu 33 C.E., pamene otsatira a Khristu anadzozedwa, chidzatha pa mapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu. w19.12 11 ¶11-12

Lachisanu, May 28

Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.—1 Akor. 15:33.

Makolo, muzithandiza ana anu kuti azicheza ndi anthu abwino. Mayi ndi bambo ayenera kudziwa anthu amene ana awo amacheza nawo komanso zimene amachita. Iwo ayeneranso kudziwa anthu amene ana awo amacheza nawo pa intaneti komanso pafoni. Zili choncho chifukwa ana anu akhoza kutengera maganizo ndi zochita za anthuwo. Makolo ambiri amayesetsa kuthandiza ana awo kuti azicheza ndi anthu amene amapereka chitsanzo chabwino potumikira Mulungu. Mwachitsanzo, N’Déni ndi Bomine, amene amakhala ku Côte d’Ivoire, ankakonda kuitana woyang’anira dera kuti azifikira kunyumba kwawo. N’Déni ananena kuti: “Zimenezi zinathandiza kwambiri mwana wathu moti iye anayamba upainiya ndipo panopa ndi woyang’anira dera wogwirizira.” Zinthu zimayenda bwino makolo akayamba kuphunzitsa ana awo adakali aang’ono. (Miy. 22:6) Chitsanzo ndi Timoteyo, amene ankayenda ndi mtumwi Paulo. Mayi ake a Timoteyo dzina lawo a Yunike ndi agogo ake dzina lawo a Loisi ankamuphunzitsa kuyambira ali “wakhanda.”​—2 Timoteyo 1:5; 3:15. w19.12 25 ¶14; 26 ¶16-17

Loweruka, May 29

Pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.​—Miy. 18:24.

Tikhale odalirika kwa anzathu. Mwachitsanzo, sitiyenera kungolonjeza kuti tidzathandiza abale ndi alongo athu pa mavuto koma tiyenera kumayesetsa kuwathandiza. (Mat. 5:37; Luka 16:10) Anthu amene akukumana ndi mavuto amalimbikitsidwa kwambiri akadziwa kuti akhoza kutidalira. Pa nkhani imeneyi, mlongo wina anati: “Zimathandiza kuti usamade nkhawa chifukwa chokayikira ngati anthu adzachitadi zimene analonjeza pa nthawi yake.” Anthu amene akumana ndi mavuto amalimbikitsidwa akafotokoza zimene zili mumtima mwawo kwa mnzawo wodalirika. Koma kuti anthu azitidalira komanso kutifotokozera zamumtima mwawo, tiyenera kukhala oleza mtima. Mlongo wina dzina lake Zhanna atasiyidwa ndi mwamuna wake, ankalimbikitsidwa akafotokozera anzake apamtima mmene ankamvera. Iye anati: “Ankandimvetsera moleza mtima ngakhale kuti mwina ndinkangobwereza zinthu zimodzimodzi.” Nanunso mukhoza kukhala odalirika kwa anzanu mukamawamvetsera moleza mtima. w20.01 10-11 ¶9-11

Lamlungu, May 30

Adzadzazidwa ndi mzimu woyera kuyambira ali m’mimba mwa mayi ake.​—Luka 1:15.

M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambiri okhulupirika omwe anapatsidwa mzimu woyera, koma sankayembekezera kupita kumwamba. Mwachitsanzo, Davide ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera. (1 Sam. 16:13) Mzimuwo unkamuthandiza kumvetsa zinthu zozama zokhudza Yehova komanso kumutsogolera polemba mbali zina za Baibulo. (Maliko 12:36) Ngakhale zili choncho, mtumwi Petulo ananena kuti Davide “sanakwere kumwamba.” (Mac. 2:34) Nayenso Yohane M’batizi ‘anadzazidwa ndi mzimu woyera.’ (Luka 1:13-16) Yesu ananena kuti panalibe wamkulu kuposa Yohane koma iye sadzapita kumwamba. (Mat. 11:10, 11) Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera pothandiza anthuwo kuchita zinthu zikuluzikulu, koma sanagwiritse ntchito mzimu wake kuti awasankhe kupita kumwamba. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti sanali okhulupirika kwambiri? Ayi. Zikungotanthauza kuti Yehova adzawaukitsa kuti adzakhale ndi moyo padzikoli.​—Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15. w20.01 23 ¶15

Lolemba, May 31

Timasonyeza chikondi, chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.​—1 Yoh. 4:19.

Yehova watilola kuti tikhale m’banja la atumiki ake. Uwutu ndi mwayi waukulu kwambiri. M’banja lathuli muli anthu amene adzipereka kwa Mulungu ndipo amasonyeza kuti amakhulupirira nsembe ya dipo ya Mwana wake. Banja lathu ndi losangalala kwambiri. Zili choncho chifukwa timakhala ndi moyo wabwino panopa komanso tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padzikoli. Chifukwa chotikonda, Yehova anakonza zoti tikhale m’banja lake ngakhale kuti zinali zovuta kwambiri. (Yoh. 3:16) Paja iye ‘anatigula pa mtengo wokwera.’ (1 Akor. 6:20) Yehova anakonza zoti dipo liperekedwe kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Choncho tili ndi mwayi woti Munthu wamkulu kwambiri m’chilengedwe chonse akhale Atate wathu. Mofanana ndi wolemba Baibulo wina, tingadzifunse kuti: “Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira?” (Sal. 116:12) Yankho la funsoli ndi lakuti palibe chimene tingamubwezere. Koma chikondi chake chimatichititsa kuti nafenso tizimukonda. w20.02 8 ¶1-3

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena