June
Lachiwiri, June 1
Mkazi mnzake wa Hana anali kum’sautsa kwambiri n’cholinga choti amukhumudwitse.—1 Sam. 1:6.
Hana, mayi ake a mneneri Samueli, anakumana ndi mavuto aakulu. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri anali wosabereka. (1 Sam. 1:2) Aisiraeli ambiri ankakhulupirira kuti ngati munthu ndi wosabereka ndiye kuti Mulungu sakumudalitsa. Choncho Hana ankachita manyazi kwambiri. (Gen. 30:1, 2) Kuwonjezera pamenepa, mwamuna wake anali ndi mkazi wina dzina lake Penina ndipo anabereka naye ana. Hana ankakhumudwa kwambiri ndi zimenezi moti ‘ankalira ndiponso sankadya.’ (1 Sam. 1:7, 10) Kodi Hana anathandizidwa bwanji? Iye anapemphera kwa Yehova n’kumuuza mmene ankamvera mumtima mwake. Atapemphera, anafotokozera nkhaniyi Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe. Ndiyeno Eli anamuuza kuti: “Pita mu mtendere, ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wam’pempha.” Ndiye chinachitika n’chiyani? Hana “anachoka ndi kupita kukadya, ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:17, 18) Kupemphera kunamuthandiza kupezanso mtendere wamumtima. w20.02 21 ¶4-5
Lachitatu, June 2
Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.—Akol. 4:6.
Posachedwapa, Yehova adzawononga dziko loipali. Anthu amene adzapulumuke ndi okhawo ‘amene ali ndi maganizo abwino owathandiza kudzapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Choncho m’pomveka kuti timafuna kuti achibale athu nawonso azitumikira Yehova. Atate wathu, yemwe ndi wachikondi, “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Tiyenera kukumbukira kuti pali njira yoyenera ndi njira yolakwika yolalikirira uthenga wabwino. Nthawi zambiri timalankhula mokoma mtima tikamalalikira anthu omwe sitiwadziwa n’komwe. Koma mwina tikhoza kulankhula mosasamala tikamalalikira achibale athu. Ambirife mwina timaona kuti sitinachite zinthu mokoma mtima pa nthawi yoyamba imene tinalalikira achibale athu ndipo mwina timanong’oneza bondo. Ndi bwino kukumbukira malangizo amene mtumwi Paulo anapereka omwe akupezeka mulemba la lero tikamathandiza achibale athu. Tikapanda kusamala, tikhoza kuwakhumudwitsa m’malo mowathandiza kuti amvetsere uthenga wathu. w19.08 14-15 ¶3-5
Lachinayi, June 3
Khristu anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.—1 Pet. 2:21.
Kodi munamva bwanji mutaphunzira mfundo zotsatirazi zokhudza Mwana? Yesu ndi wachiwiri kwa Wolamulira wa chilengedwe chonsechi. Iye anapereka moyo wake kuti ukhale dipo lotiwombola ndipo anachita zimenezi ndi mtima wonse. Kukhulupirira dipo kungathandize kuti machimo athu akhululukidwe, tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso tidzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wathu. Iye amafuna kutithandiza kuti tipeze madalitso chifukwa cha dipo komanso tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. (Aheb. 4:15; 7:24, 25) Iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo Yehova adzamugwiritsa ntchito kuti ayeretse dzina lake, athetse zoipa zonse komanso abweretse madalitso osatha padzikoli. (Mat. 6:9, 10; Chiv. 11:15) Yesu ndi chitsanzo chathunso. Iye anapereka chitsanzo chabwino podzipereka ndi mtima wonse kuti achite chifuniro cha Mulungu. (Yoh. 4:34) Munthu akakhulupirira zimene Baibulo limanena zokhudza Mwana wa Mulungu amayamba kumukonda kwambiri. Ndiye chikondi chimenechi n’chimene chingakulimbikitseni kuti muzichita chifuniro cha Mulungu pa moyo wanu ngati mmene Yesu anachitira. w20.03 10 ¶12-13
Lachisanu, June 4
Muzipemphera mosalekeza.—1 Ates. 5:17.
Yesu ankakonda kupemphera nthawi yonse imene anali padzikoli. Pa tsiku limene anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake, iye anapempherera mkate ndi vinyo. (1 Akor. 11:23-25) Asanachoke pamalo amene anachitira mwambo wa Pasika, Yesu anapempheranso ndi ophunzira ake. (Yoh. 17:1-26) Atafika kuphiri la Maolivi usiku, iye anapemphera mobwerezabwereza. (Mat. 26:36-39, 42, 44) Ndipo mawu omaliza amene Yesu ananena asanafe analinso pemphero. (Luka 23:46) Choncho tingati iye ankaganizira za Yehova pa chinthu chilichonse chachikulu chimene chinkachitika pa tsikulo. Chinthu chimodzi chimene chinathandiza Yesu kuti apirire bwinobwino mavuto ake n’chakuti ankapemphera kwa Atate ake. Koma usiku woti aphedwa mawa lake, atumwi ake sanalimbikire kupemphera. Izi zinachititsa kuti achite mantha kwambiri pamene anakumana ndi mayesero aakulu. (Mat. 26:40, 41, 43, 45, 56) Choncho kuti nafenso tikhalebe okhulupirika tikakumana ndi mavuto tiyenera ‘kupemphera kosalekeza.’ w19.04 9 ¶4-5
Loweruka, June 5
Ine ndine Yehova, sindinasinthe.—Mal. 3:6.
Yehova amadana kwambiri ndi kukhulupirira mizimu. Paja anauza Aisiraeli kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deut. 18:10-12) Akhristu sayendera Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli. Koma maganizo a Yehova pa nkhani yokhulupirira mizimu sanasinthe. Yehova amatichenjeza pa nkhani yokhulupirira mizimu chifukwa amadziwa kuti imeneyi ndi njira imene Satana akupusitsira anthu. Satana amagwiritsa ntchito njirayi pofuna kuti anthu azikhulupirira kuti munthu akafa amakakhalanso ndi moyo kwinakwake. (Mlal. 9:5) Kukhulupirira mizimu kumachititsanso kuti anthu azikhala mwamantha n’kusiya kutumikira Yehova. Cholinga cha Satana n’chakuti anthu azidalira mizimu yoipa m’malo modalira Yehova. w19.04 21 ¶5-6
Lamlungu, June 6
Ngati ukuchita zoipa, chita mantha.—Aroma 13:4.
Kugwirira mwana ndi tchimo lalikulu kwambiri. Munthu amene wagwirira mwana amapweteka mwanayo koopsa. Iye amachititsa mwanayo kumva kuti si wotetezeka ndiponso kuti asamakhulupirire anthu. Choncho ana ayenera kutetezedwa kuti zoipazi zisawachitikire ndipo anthu amene agwiriridwa amafunika kulimbikitsidwa komanso kuthandizidwa. (1 Ates. 5:14) Munthu wamumpingo akagwirira mwana, amaipitsa mbiri ya mpingo. (Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12) Sitimalekerera anthu amene aipitsa mbiri yabwino ya mpingo chifukwa chochita tchimo lalikulu ndipo sanalape. Munthu wamumpingo akaphwanya lamulo la dziko pochita zinthu monga kugwirira mwana ndiye kuti wachimwira boma. (Yerekezerani ndi Machitidwe 25:8.) Ngakhale kuti si udindo wa akulu kuimba munthu mlandu chifukwa chophwanya malamulo a boma, sateteza munthu yemwe wagwirira mwana kuti asaimbidwe mlandu ndi bomalo. w19.05 9 ¶4-7
Lolemba, June 7
Kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa.—1 Akor. 3:19.
Anthufe tikhoza kupirira kapena kuthana ndi vuto lililonse chifukwa chakuti Yehova ndi Mlangizi wathu wamkulu. (Yes. 30:20, 21) Mawu ake amatipatsa zinthu zonse zofunika kuti munthu akhale “woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:17) Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo timakhala anzeru kuposa anthu amene amaona kuti ndi bwino kutsatira “nzeru za m’dzikoli.” (Sal. 119:97-100) N’zomvetsa chisoni kuti nzeru za m’dzikoli zimagwirizana ndi zimene anthufe timalakalaka. Choncho tingamavutike kupewa kuganiza komanso kuchita zinthu zimene anthu a m’dzikoli amaganiza ndi kuchita. M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.” (Akol. 2:8) Mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera zokhudza masiku otsiriza, anthu anayamba kukhala “okonda zosangalatsa.” (2 Tim. 3:4) Kufala kwa matenda opatsirana pogonana monga Edzi kumapereka umboni wakuti nzeru za m’dzikoli ndi zopusa.—2 Pet. 2:19. w19.05 21 ¶1-2; 22 ¶4-5
Lachiwiri, June 8
Musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.—Aef. 6:11.
Satana anachititsa Aisiraeli kuganiza kuti zinthu zingawayendere bwino ngati atatengera zimene anthu a m’dzikolo ankachita. Anthuwo ankakhulupirira kuti pamafunika kuchita miyambo ina kuti milungu yawo ibweretse mvula. Aisiraeli amene sankadalira Yehova ankakhulupiriranso kuti kuchita nawo miyambo yolemekeza Baala n’kumene kukanathandiza kuti apewe chilala. Satana anagwiritsanso ntchito chilakolako chawo cha kugonana. Anthu a m’dzikolo ankachita chiwerewere akamalambira milungu yawo. Iwo anafika pokhala ndi mahule aakazi ndi aamuna apakachisi. Sankaona vuto lililonse ndi zinthu zoipa monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (Deut. 23:17, 18; 1 Maf. 14:24) Anthuwo ankaganiza kuti zimenezi zinkathandiza kuti milungu yawo ichititse nthaka kukhala yachonde. Aisiraeli ambiri anakopeka ndi miyambo yachiwerewereyo moti anayamba kulambira milungu yonyenga. w19.06 2 ¶3; 4 ¶7-8
Lachitatu, June 9
Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.—Aheb. 6:10.
Pali abale ndi alongo ambiri omwe ankatumikira pa Beteli kapena pa utumiki wina ndipo anasinthidwa. Ziyenera kuti zinali zowawa kwambiri kwa abale ndi alongo okhulupirikawa kusiya utumiki womwe ankaukonda. Ngati zimenezi zakuchitikirani inuyo, kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Muziwerenga Malemba tsiku lililonse komanso kuwaganizira mozama kuti mukhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Muyeneranso kupitiriza kulalikira mwakhama uthenga wabwino mumpingo wanu watsopano. Yehova saiwala anthu amene amapitiriza kumutumikira mokhulupirika ngakhale kuti sangachite zambiri ngati kale. Muzikhala moyo wosalira zambiri. Musalole kuti nkhawa zam’dziko la Satanali zikulepheretseni kutumikira Yehova. (Mat. 13:22) Musalolenso anzanu, achibale anu kapena anthu ena kuti akukakamizeni kufunafuna chuma m’dziko la Satanali. (1 Yoh. 2:15-17) Muzidalira Yehova yemwe analonjeza kuti adzakuthandizani pa nthawi yoyenera kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba, mukhale osangalala komanso mukhale ndi zinthu zonse zofunika pa moyo wanu.—Aheb. 4:16; 13:5, 6. w19.08 20 ¶4; 21-22 ¶7-8
Lachinayi, June 10
Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.—Sal. 55:22.
Kodi inunso mukukumana ndi mavuto amene akukudetsani nkhawa? N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amamvetsa mmene timamvera. Iye amadziwa zimene sitingakwanitse, zimene tikuganiza komanso zimene zili mumtima mwathu. (Sal. 103:14; 139:3, 4) Tikamadalira Yehova, adzatithandiza kupirira mavuto athu. Tikakhala ndi nkhawa, tingayambe kuganiza kuti mavuto athu sangathe. Izi zikakuchitikirani, muzikumbukira kuti Yehova adzakuthandizani. Kodi angakuthandizeni bwanji? Iye amakupemphani kuti muzimuuza zimene zikukudetsani nkhawa ndipo amalonjeza kuti adzayankha mapemphero anu. (Sal. 5:3; 1 Pet. 5:7) Choncho muzikonda kupemphera n’kumauza Yehova mavuto anu. Si kuti adzalankhula nanu mwachindunji koma adzakulankhulani kudzera m’Mawu ake komanso gulu lake. Nkhani za m’Baibulo zingakulimbikitseni komanso kukuthandizani kukhala ndi chiyembekezo. Nawonso abale ndi alongo anu angakulimbikitseni kwambiri.—Aroma 15:4; Aheb. 10:24, 25. w19.06 16 ¶7-8
Lachisanu, June 11
Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.—Mat. 24:9.
Mukamazunzidwa muzipemphera kwa Yehova ndipo muyenera ‘kukhuthula mtima wanu ngati madzi’ n’kuuza Atate wanu wachikondi zonse zimene zikukuchititsani mantha kapena kukudetsani nkhawa. (Maliro 2:19) Mukamakonda kupemphera chonchi, ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba kwambiri. (Aroma 8:38, 39) Musamakayikire madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse. (Num. 23:19) Ngati simukhulupirira malonjezo a Mulungu ndi mtima wonse, Satana ndi anthu ake sangavutike kukuchititsani mantha. (Miy. 24:10; Aheb. 2:15) Mungachite bwino kupeza nthawi yofufuza ndi kuganizira malonjezo a Mulungu okhudza Ufumu komanso zimene zimakutsimikizirani kuti malonjezowo adzakwaniritsidwa. Kodi zimenezi zingakuthandizeni bwanji? Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Stanley Jones, yemwe anali m’ndende kwa zaka 7 chifukwa cha chikhulupiriro chake. N’chiyani chinamuthandiza kupirira n’kukhalabe wokhulupirika? Iye anati: “Kudziwa bwino za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuukhulupirira ndi mtima wonse n’kumene kunandithandiza kuti ndikhalebe wokhulupirika.” Ngati mumakhulupirira malonjezo a Mulungu ndi mtima wonse, simungachite mantha.—Miy. 3:25, 26. w19.07 2 ¶1; 3 ¶6-7
Loweruka, June 12
Mukalowa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera, ndipo mukhalebe momwemo kufikira nthawi yochoka.—Mat. 10:11.
N’chifukwa chiyani ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi yofunika kwambiri? Zili choncho chifukwa ophunzira a Khristu okha ndi amene angakhale anzake a Mulungu. Komanso anthu amene amatsatira Khristu amakhala ndi moyo wabwino panopa ndipo amayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’tsogolo. (Yoh. 14:6; 17:3) Kunena zoona, Yesu watipatsa udindo waukulu kwambiri. Koma sitigwira ntchitoyi patokha. Ponena za iyeyo komanso anzake ena, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Anthufe si angwiro koma Yehova ndi Khristu anatipatsa mwayi waukulu kwambiri. Ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi yosangalatsa kwambiri. Chinthu choyamba pa ntchito yathuyi ndi ‘kufufuza’ anthu amene ali ndi mtima wabwino. Tikamayesetsa kuchitira umboni kwa anthu onse amene timakumana nawo, timasonyeza kuti ndifedi Mboni za Yehova. Ndipo tikamatsatira lamulo la Khristu lakuti tizilalikira, timasonyeza kuti ndife Akhristu enieni. w19.07 15 ¶3-5
Lamlungu, June 13
Nzeru zimateteza monga mmene ndalama zimatetezera, koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.—Mlal. 7:12.
Anthu ambiri amachita chidwi ndi mfundo zothandiza za m’Baibulo. Chitsanzo ndi zimene mlongo wina wa ku New York ananena. Iye amalalikira kwa anthu olankhula Chitchainizi ndipo anati: “Ndimayesetsa kusonyeza chidwi kwa anthu ndipo ndimamvetsera maganizo awo. Ndikamva kuti angofika kumene kuchokera kudziko lina, ndimawafunsa kuti: ‘Panopa zikukuyenderani bwanji kunoko? Mwapeza kale ntchito? Kaya mukukhala bwanji ndi anthu akuno?’” Nthawi zina zimenezi zimathandiza mlongoyu kuti ayambe kukambirana nawo mfundo za m’Baibulo. Mwina angawafunse kuti: “Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingatithandize kugwirizana ndi anthu ena? Kodi mungakonde kuti ndikusonyezeni mwambi wina wa m’Baibulo? Umanena kuti: ‘Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Choncho mkangano usanabuke, chokapo.’ Kodi mukuganiza kuti malangizo amenewa angatithandize kuti tizikhala bwino ndi anzathu?” (Miy. 17:14) Kucheza ndi anthu m’njira ngati imeneyi kungatithandize kuzindikira anthu amene angafune kuphunzira zambiri. w19.07 23 ¶13
Lolemba, June 14
Kodi zingakhale bwanji munthu mmodzi atagwa popanda wina woti am’dzutse?—Mlal. 4:10.
Utumiki ukasintha, chimene anthu amafuna kwambiri ndi kuwamvetsa osati kumangodandaula ndi zimene zawachitikira. Mwina akuvutika chifukwa cha matenda awo kapena a wachibale wawo. Mwinanso angakhale ndi chisoni chifukwa cha imfa ya mnzawo kapena wachibale wawo. Akhozanso kumadandaula, mwina akakhala kwaokha, chifukwa choti akusowana ndi abale ndi alongo am’dera limene ankatumikira. Kuti maganizo a anthu ngati amenewa akhale m’malo, zingatenge nthawi yaitali. Zimene inuyo mungachitire anthu oterewa komanso chitsanzo chanu zikhoza kuwathandiza kuti azolowere moyo watsopano. Mlongo wina amene anatumikira m’dziko lina kwa zaka zambiri anati: “Pamene ndinkachita utumiki, ndinkachititsa maphunziro a Baibulo tsiku lililonse. Koma utumikiwu utasintha, zinkandivuta ngakhale kungowerenga lemba kapena kuonetsa vidiyo mu utumiki. Chosangalatsa n’chakuti abale ndi alongo ankanditenga ku maulendo obwereza kapena maphunziro awo. Zonsezi zinandithandiza kuti ndiyambenso kukhala wosangalala.” w19.08 22 ¶10; 24 ¶13-14
Lachiwiri, June 15
Ndikudandaulira Eodiya ndi Suntuke, kuti akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.—Afil. 4:2.
Mofanana ndi Eodiya ndi Suntuke, ifenso tikhoza kulephera kukonda kwambiri abale athu chifukwa choti timangoganizira zimene amalakwitsa. Koma tizikumbukira kuti aliyense amalakwitsa zinthu tsiku ndi tsiku. Choncho tikamangoganizira zimene ena amalakwitsa, tikhoza kusiya kuwakonda. Mwachitsanzo, tikhoza kukhumudwa ngati m’bale wina waiwala kuthandiza nawo poyeretsa Nyumba ya Ufumu. Ndiye tikayamba kuganizira zinthu zina zimene m’baleyo analakwitsanso mkwiyo wathu ukhoza kuwonjezeka ndipo tingasiye kumukonda. Zoterezi zikakuchitikirani, muzikumbukira mfundo iyi: Yehova amaona zimene ifeyo timalakwitsa komanso zimene m’bale wathuyo amalakwitsa. Ngakhale zili choncho, iye amatikonda tonse. Choncho ndi bwino kutsanzira chikondi cha Yehova n’kumaona zabwino zimene anzathu amachita. Tikamayesetsa kuti tizikonda abale athu tidzayamba kugwirizana nawo kwambiri.—Afil. 2:1, 2. w19.08 9-10 ¶7-8
Lachitatu, June 16
Yehova . . . amaona wodzichepetsa.—Sal. 138:6.
Yehova amakonda anthu odzichepetsa. Ndipo anthu odzichepetsa okha ndi amene angakhale naye pa ubwenzi wolimba. Koma munthu “wodzikuza samuyandikira.” Tonsefe timafuna kuti tizisangalatsa Yehova komanso kuti iye azitikonda. Choncho tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa. Kudzichepetsa kumatanthauza kukhala ndi mtima wosadzikweza kapena wosanyada. Baibulo limasonyeza kuti munthu wodzichepetsa amakhala ndi maganizo oyenera podziyerekezera ndi Yehova Mulungu komanso anzake. Iye amazindikira kuti munthu aliyense amamuposa m’njira inayake. (Afil. 2:3, 4) Anthu ena amaoneka ngati odzichepetsa chifukwa choti ndi aphee. Apo ayi, amasonyeza ulemu chifukwa cha chikhalidwe chawo kapena mmene makolo awo anawalerera. Koma pansi pa mtima akhoza kukhala anthu odzikuza kwambiri. Ndipo zinthu zina zikachitika khalidwe lawo lenileni limaonekera.—Luka 6:45. w19.09 2 ¶1, 3-4
Lachinayi, June 17
Adzabwezera chilango kwa anthu . . . osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.—2 Ates. 1:8.
“Uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu” umatanthauza zinthu zonse zimene iye anaphunzitsa. Timasonyeza kuti timamvera uthenga wabwino tikamatsatira mfundo zake pa moyo wathu. Timasonyezanso kumvera tikamaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, kutsatira mfundo zachilungamo za Mulungu komanso kuuza ena za Ufumu wa Mulungu. (Mat. 6:33; 24:14) Kuwonjezera pamenepa, timathandiza Akhristu odzozedwa kugwira ntchito yaikulu imene anapatsidwa. (Mat. 25:31-40) Posachedwapa, odzozedwawa adzasonyeza kuyamikira zinthu zabwino zimene a “nkhosa zina” awachitira. (Yoh. 10:16) Kodi adzachita bwanji zimenezi? Nkhondo ya Aramagedo isanayambe, odzozedwa onse okwana 144,000 adzakhala atapita kumwamba ndipo adzakhala ndi matupi auzimu osakhoza kufa. Iwo adzakhala m’gulu la asilikali akumwamba amene adzawononge Gogi n’kupulumutsa “khamu lalikulu” la anthu a Mulungu. (Chiv. 2:26, 27; 7:9, 10) Choncho ndi mwayi waukulu kuthandiza atumiki a Yehova odzozedwa pa nthawi imene adakali padziko lapansi. w19.09 12-13 ¶16-18
Lachisanu, June 18
Mudzatsitsimulidwa.—Mat. 11:29.
Kodi ntchito imene Yesu anatipatsa imatitsitsimula bwanji? Imatitsitsimula chifukwa tili ndi oyang’anira abwino kwambiri. Woyang’anira wathu wamkulu ndi Yehova ndipo iye si wosayamika kapena wankhanza. Koma amayamikira ntchito imene timagwira. (Aheb. 6:10) Amatipatsanso mphamvu kuti tigwire bwino ntchito yathu. (2 Akor. 4:7; Agal. 6:5) Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu, amapereka chitsanzo chabwino kwambiri. (Yoh. 13:15) Nawonso akulu amene amatiyang’anira amayesetsa kutsanzira Yesu yemwe ndi “m’busa wamkulu.” (Aheb. 13:20; 1 Pet. 5:2) Iwo amatidyetsa komanso kutiteteza. Pochita zimenezi amayesetsa kukhala olimbikitsa, okoma mtima komanso olimba mtima. Komanso tili ndi anzathu abwino kwambiri. Palibenso anthu ena amene ali ndi anzawo achikondi amene angagwire nawo ntchito mogwirizana ngati mmene zilili ndi ifeyo. Tangoganizani: Tili ndi mwayi wogwira ntchito limodzi ndi anthu amakhalidwe abwino kwambiri koma omwe sadziona ngati apamwamba. Iwo amaona kuti anthu ena ndi owaposa. Iwo amationa ngati anzawo apamtima osati anthu ongogwira nawo ntchito. Iwo amatikonda kwambiri moti angalolere kutifera. w19.09 20 ¶1; 23 ¶12-14
Loweruka, June 19
Inu abale simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.—1 Ates. 5:4.
M’malangizo ake, Paulo anatchula “tsiku la Yehova.” (1 Ates. 5:1-6) Apa ankanena za nthawi imene idzayambe ndi kuukiridwa kwa “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, ndipo idzatha ndi nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16; 17:5) Paulo anatchulanso zinthu zina zimene zingatithandize kukonzekera “tsiku la Yehova.” Ananena kuti “tisapitirize kugona ngati mmene enawo akuchitira.” Koma ananena kuti “tikhalebe maso”kuti tisayambe kukopeka ndi nkhani zandale. Ngati tingayambe kuchita nawo zandale, ndiye kuti tikhoza kukhala “mbali ya dzikoli.” (Yoh. 15:19) Tizikumbukira kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungabweretse mtendere padziko lonse. Tiyeneranso kuthandiza anthu ena kuti akhale maso n’kumadziwa zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika padzikoli. Chisautso chachikulu chikangoyamba, mwayi woti anthu ayambe kutumikira Yehova udzakhala utatha. N’chifukwa chake tiyenera kulalikira mwakhama. w19.10 8 ¶3; 9 ¶5-6
Lamlungu, June 20
Tenga mpukutu ndi kulembamo mawu onse amene ndakuuza okhudza chilango chimene ndidzapatsa Isiraeli [ndi] Yuda.—Yer. 36:2.
Atamaliza kulemba machenjezo mumpukutu, Yeremiya anafunika kudalira Baruki kuti akapereke uthengawu. (Yer. 36:5, 6) Baruki anachita zimenezi molimba mtima ngakhale kuti zinaika moyo wake pa ngozi. Yeremiya ayenera kuti ananyadira kwambiri pamene Baruki anapita kubwalo la kachisi kukapereka uthengawu. (Yer. 36:8-10) Akalonga a ku Yuda atamva zimene Baruki anachita anamulamula kuti awawerengerenso mpukutuwo mokweza. (Yer. 36:14, 15) Kenako akalongawo anasankha zokauza Mfumu Yehoyakimu zimene Yeremiya ananena. Mfumu Yehoyakimu anakwiya kwambiri atamva uthengawo moti anawotcha mpukutuwo n’kulamula kuti Yeremiya ndi Baruki amangidwe. Koma Yeremiya anangotenga mpukutu wina n’kupatsa Baruki ndipo anayamba kumuuzanso uthenga wa Yehova woti alembe. Ndiye Baruki analemba “mawu onse amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha.”—Yer. 36:26-28, 32. w19.11 3-4 ¶4-6
Lolemba, June 21
Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.
Yehova akhoza kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse cholinga chake. Mwachitsanzo, iye amatha kukhala Mphunzitsi, Wotonthoza ndiponso Mlaliki. (Yes. 48:17; 2 Akor. 7:6; Agal. 3:8) Ngakhale zili choncho, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito anthu kuti akwaniritse cholinga chake. (Mat. 24:14; 28:19, 20; 2 Akor. 1:3, 4) Yehova angatipatsenso nzeru ndi mphamvu kuti tikwanitse kuchita zimene iye akufuna. Zonsezi zikugwirizana ndi zimene akatswiri ambiri amanena pofotokoza tanthauzo la dzina lake lakuti Yehova. Tonsefe timafuna kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova koma ena amakayikira ngati iye angawagwiritse ntchito. Amatero chifukwa chakuti amaona kuti ndi achikulire, alibe luso kapena zinthu sizili bwino pa moyo wawo. Ndiye pali anthu ena amene amaona kuti zimene akuchita n’zokwanira ndipo palibe chifukwa choti aziyesetsa kuchita zambiri. w19.10 20 ¶1-2
Lachiwiri, June 22
Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.—1 Tim. 6:10.
Kukonda chuma kungatisokoneze komanso kufooketsa chikhulupiriro chathu. Mtumwi Paulo anati: “Msilikali amene ali pa nkhondo sachita nawo zamalonda zimene anthu wamba amachita, pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali.” (2 Tim. 2:4) Asilikali a Chiroma sankaloledwa kuti azichita zamalonda ngakhale pang’ono. Nafenso tisamalole kusokonezedwa ndi zinthu zina moti n’kulephera kusangalatsa Yehova ndi Khristu, amene ndi Atsogoleri athu. Tiyenera kuona kuti zimenezi n’zofunika kwambiri kuposa chilichonse chimene tingapeze m’dziko la Satanali. Choncho tizionetsetsa kuti tili ndi nthawi ndiponso mphamvu zokwanira kuti tizitumikira Yehova komanso kusamalira chishango chathu chachikhulupiriro ndi zida zina zauzimu. Nthawi zonse tiyenera kukhala maso. Paja mtumwi Paulo anachenjeza kuti ‘anthu ofunitsitsa kulemera adzasocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro.’—1 Tim. 6:9, 10. w19.11 17 ¶12, 14-15
Lachitatu, June 23
Chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.—1 Ates. 5:3.
Tsiku la Yehova” lisanafike anthu adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:1-6) Pa 1 Atesalonika 5:2, mawu oti “tsiku la Yehova” akunena za ‘chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:14) Kodi tidzadziwa bwanji kuti chisautsochi chatsala pang’ono kuyamba? Baibulo limafotokoza za uthenga winawake wapadera umene udzalengezedwe. Uthengawu udzakhala chizindikiro chakuti chisautso chachikulu chatsala pang’ono kuyamba. Uthenga umene udzalengezedwewo udzakhala wakuti “bata ndi mtendere.” Kodi atsogoleri a zipembedzo adzalengeza nawo uthengawu? Mwina adzatero. Mulimonse mmene zidzakhalire, mawuwa adzangokhala uthenga wina wouziridwa ndi ziwanda. Koma uthenga wabodzawu udzakhala woopsa chifukwa chakuti udzachititsa anthu kuganiza kuti ndi otetezeka pa nthawi imene chisautso chachikulu kwambiri chatsala pang’ono kuyamba. Paja Baibulo limanena kuti “chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati.” Koma kodi n’chiyani chidzachitikire atumiki okhulupirika a Yehova? Mwina akhoza kudzadabwa kuti tsiku la Yehova layamba modzidzimutsa kwambiri, koma adzakhala atakonzeka. w19.09 9 ¶7-8
Lachinayi, June 24
Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . nthawi yofunafuna ndi nthawi yovomereza kuti chinthu chatayika.—Mlal. 3:1, 6.
Mukamasankha zochita, muzidziwa bwinobwino zimene mukufuna kuchita. Mukhoza kumaliza zimene mwayamba ngati mukudziwa bwinobwino zimene mukufuna kuchita. Mwachitsanzo, mwina mwasankha kuti muziwerenga Baibulo pafupipafupi. Koma ngati simunasankhe nthawi imene mukufuna kuti muziliwerenga, mwina simungakwaniritse cholinga chanucho. Akulunso angasankhe kuti azichita maulendo aubusa pafupipafupi. Koma patapita nthawi, angapezeke kuti sakuchita zimene anasankhazo. Kuti akwaniritse zimene anasankha, angachite bwino kudzifunsa mafunso awa: “Kodi ndi abale ndi alongo ati amene akufunikira kulimbikitsidwa kwambiri? Nanga tasankha nthawi yeniyeni yoti tiwayendere?” Muzidziwanso zimene mungakwanitse. Palibe munthu amene ali ndi nthawi, zinthu kapena mphamvu zokwanira zoti azichitira chilichonse chimene akufuna. Choncho muyenera kudziwa zimene mungakwanitse kuchita. Ndipo nthawi zina mungafunike kusintha zimene munasankha chifukwa choti simungakwanitse kuzichita. w19.11 29 ¶11-12
Lachisanu, June 25
Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu, ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.—Chiv. 7:14.
Pa Yesaya 65:21-23 pali ulosi wonena mmene moyo udzakhalire padzikoli. Pa nthawiyo palibe amene adzakhale wosowa zochita. Baibulo limasonyeza kuti anthu a Mulungu azidzagwira ntchito zosangalatsa komanso zothandiza. Pamapeto pa zaka 1,000 zimenezi, chilengedwechi “chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Yehova anakonza zoti Aisiraeli azigwira ntchito komanso kupuma. Ndi mmene zidzakhalirenso ndi anthu ake mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Tidzakhala ndi nthawi yokwanira yolambira Mulungu. Paja kulambira Mulungu n’kumene kumatithandiza kuti tizisangalala panopa ndipo ndi mmene zidzakhalirenso m’dziko latsopano. Anthu onse okhulupirika adzasangalala kwambiri mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu chifukwa chakuti adzakhala ndi ntchito zosangalatsa komanso azidzatumikira Mulungu momasuka. w19.12 12 ¶15; 13 ¶17-18
Loweruka, June 26
Mawu awa . . . azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomereza mwa ana ako.—Deut. 6:6, 7.
“Kukhomereza” kumatanthauza “kuphunzitsa ndi kukumbutsa mobwerezabwereza.” Kuti zimenezi zitheke, makolo ayenera kukhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi ana awo. Nthawi zina, kulangiza ana mobwerezabwereza kungaoneke kotopetsa. Komabe makolo ayenera kuona kuti imeneyi ndi njira yothandizira ana awo kumvetsa Mawu a Mulungu komanso kuwagwiritsa ntchito. Ndiye mukufunika kuti muziwadziwa bwino ana anu. Lemba la Salimo 127 limayerekezera ana ndi mivi. (Sal. 127:4) Mofanana ndi mivi imene imapangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana komanso imasiyana kukula kwake, ananso amakhala osiyana. Choncho makolo ayenera kudziwa mmene angaphunzitsire mwana aliyense. Banja lina la ku Israel lomwe linalera bwino ana awo awiri kuti azitumikira Yehova linafotokoza zimene zinawathandiza. Iwo anati: “Tinkaphunzira ndi mwana aliyense payekha.” Munthu aliyense amene ndi mutu wa banja angasankhe ngati zimenezi zingathandize. w19.12 26-27 ¶18-20
Lamlungu, June 27
Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.—Mat. 7:12.
Tikakumana ndi mavuto, timayamikira kwambiri ngati anthu ena atithandiza. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Ryan amene bambo ake anafa pa ngozi. Iye anati: “Munthu ukakhala pamavuto, zinthu zina za tsiku ndi tsiku zimakhala zovuta. Ndiye anthu akakuchitira zinthu ngakhale zitakhala zazing’ono, zimakuthandiza kwambiri.” Dziwani kuti zimene mungachitire anthu ena pa nthawi yamavuto, ngakhale zitakhala zochepa, zingawathandize kwambiri. Maliko ayenera kuti ankatanganidwa ndithu. Koma ankayesetsa kulimbikitsa mtumwi Paulo moti Pauloyo anali womasuka kupempha kuti iye amuthandize. Mlongo wina dzina lake Angela anayamikira kwambiri pamene anthu ena anamulimbikitsa wachibale wake ataphedwa. Iye anati: “Anthu amene ali ndi mtima wofuna kuthandiza amakhala osavuta kulankhula nawo ndipo samangika kapena kukayikira pothandiza anzawo.” Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndili ndi mtima wofuna kuthandiza anthu ena pa mavuto awo?’ w20.01 11-12 ¶14-16
Lolemba, June 28
Aliyense wakudya mkatewu kapena kumwa za m’kapu ya Ambuye mosayenerera, adzakhala ndi mlandu.—1 Akor. 11:27.
Kodi Mkhristu wodzozedwa angadye bwanji zizindikiro “mosayenerera” pa Chikumbutso? Iye angachite zimenezi ngati atadya zizindikirozo koma asakutsatira mfundo za Yehova. (Aheb. 6:4-6; 10:26-29) Odzozedwa amadziwa kuti ayenera kukhalabe okhulupirika ngati akufuna kupeza “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.” (Afil. 3:13-16) Mzimu woyera wa Yehova umathandiza atumiki ake kuti akhale odzichepetsa osati onyada. (Aef. 4:1-3; Akol. 3:10, 12) Choncho odzozedwa sadziona kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena. Iwo amadziwa kuti Yehova sapereka kwambiri mzimu woyera kwa odzozedwa kuposa atumiki ake ena. Saganiza kuti iwo amamvetsa bwino mfundo za m’Baibulo kuposa Akhristu ena. Sangauzenso munthu wina kuti nayenso wadzozedwa ndipo ayenera kuyamba kudya zindikiro pa Chikumbutso. M’malomwake, amazindikira kuti Yehova yekha ndi amene amasankha anthu kuti apite kumwamba. w20.01 27-28 ¶4-5
Lachiwiri, June 29
Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.—Yak. 4:8.
Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba komanso tizilankhulana naye. Amatilimbikitsa kuti ‘tizilimbikira kupemphera’ ndipo nthawi zonse amakhala wokonzeka kumva mapemphero athu. (Aroma 12:12) Iye sangatope kapena kutanganidwa kwambiri moti sangatimvetsere. Ifenso timamumvetsera tikamawerenga Baibulo komanso mabuku otithandiza kulimvetsa. Timamvanso mawu ake tikamamvetsera pamisonkhano. Tikamalankhula ndi Yehova komanso kumumvetsera nthawi zonse ubwenzi wathu umalimba. Yehova amafuna kuti tikamapemphera tizikhuthula zamumtima mwathu. (Sal. 62:8) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mapemphero anga amakhala ngati uthenga umene ndangokopera? Kapena amakhala ngati uthenga umene ndaulemba mochokera mumtima?’ N’zosachita kufunsa kuti mumakonda kwambiri Yehova ndipo mumafuna kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kumalankhula naye pafupipafupi. Muzimuuza zakukhosi kwanu, zimene zikukusangalatsani komanso zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipo musamakayikire kuti iye adzakuthandizani mukamupempha kuti akuthandizeni. w20.02 9 ¶4-5
Lachitatu, June 30
Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu.—1 Pet. 5:2.
Yehova wapereka kwa akulu udindo wofunika woyang’anira anthu ake. Ndipo akulu angaphunzire zambiri kwa Nehemiya pa nkhani yoyang’anira anthu a Yehova. Nehemiya anali ndi udindo waukulu chifukwa anali bwanamkubwa ku Yuda. (Neh. 1:11; 2:7, 8; 5:14) Taganizirani za mavuto amene ankakumana nawo. Iye anaona kuti anthu aipitsa kachisi komanso sankatsatira Chilamulo pa nkhani yothandiza Alevi kupeza zofunika pa moyo. Ayuda sankasunganso Sabata komanso anakwatira akazi amitundu ina. Ndiye kodi Nehemiya anatani ataona mavuto amenewa? (Neh. 13:4-30) Nehemiya sankagwiritsa ntchito molakwika udindo wake pokakamiza anthu a Mulungu kuti aziyendera maganizo ake. M’malomwake, ankapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kuti azimuthandiza komanso ankaphunzitsa anthu Chilamulo cha Yehova. (Neh. 1:4-10; 13:1-3) Iye anadzichepetsanso n’kumagwira ntchito ndi abale ake yomanga mpanda wa Yerusalemu.—Neh. 4:15. w19.09 16 ¶9-10