August
Lamlungu, August 1
Amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha.—Yoh. 8:29.
Yesu anakhalabe ndi mtendere mumtima pamene ankazunzidwa chifukwa ankadziwa kuti akusangalatsa Atate ake. Iye anakhalabe womvera ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri. Iye ankakonda kwambiri Atate ake ndipo chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake chinali kutumikira Yehova. Yesu asanabwere padzikoli anali “mmisiri waluso” wa Yehova. (Miy. 8:30) Ali padzikoli, iye ankalalikira mwakhama mfundo zokhudza Atate ake. (Mat. 6:9; Yoh. 5:17) Yesu ankasangalala kwambiri kugwira ntchito imeneyi. (Yoh. 4:34-36) Ifenso tingatsanzire Yesu pomvera Yehova komanso kukhala ndi “zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) ‘Tikamatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira’ timayamba kuona mavuto athu m’njira yoyenera. (Mac. 18:5) Mwachitsanzo, anthu amene timawalalikira nthawi zambiri amakumana ndi zinthu zoipa kuposa ifeyo. Koma akayamba kukonda Yehova komanso kutsatira malangizo ake, amasintha kwambiri n’kukhala osangalala. Ndiye nthawi iliyonse imene taona zimenezi, zimatitsimikizira kuti Yehova adzatisamalira zivute zitani. w19.04 10-11 ¶8-9
Lolemba, August 2
Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.—Mac. 19:19.
Anthuwa anaona kuti m’pofunika kusiyiratu kuchita zamizimu. Mabuku awo anali odula kwambiri. Koma m’malo mopatsa anthu ena kapena kuwagulitsa, anawawononga. Iwo ankaganizira kwambiri zosangalatsa Yehova osati mtengo wa mabukuwo. Kodi tingatsanzire bwanji Akhristu amenewa? Ndi bwino kutaya chinthu chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. Apa tikutanthauza zinthu monga zithumwa, mankhwala otsirikira kapena chinthu chilichonse chimene anthu amavala kapena kukhala nacho pofuna kudziteteza ku mizimu yoipa. (1 Akor. 10:21) Tizisankha bwino zosangalatsa. Tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosangalatsa zilizonse zimene ndimakonda zimakhudzana ndi zamizimu? Tikamasankha zosangalatsa tiyenera kupewa chilichonse chimene Yehova amadana nacho. Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti ‘tisapalamule chilichonse kwa Mulungu.’—Mac. 24:16. w19.04 22-23 ¶10-12
Lachiwiri, August 3
Aitane akulu.—Yak. 5:14.
Akulu akamva kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu ayenera kuganizira mfundo zambiri. Iwo amaganizira kwambiri zimene angachite kuti dzina la Mulungu lisadetsedwe. (Lev. 22:31, 32; Mat. 6:9) Iwo amaganiziranso zoteteza abale ndi alongo mwauzimu ndiponso amayesetsa kuthandiza aliyense amene walakwiridwa. Ngati wochimwayo ndi munthu wamumpingo, akulu amaganiziranso zomuthandiza kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova, ngati n’zotheka. (Yak. 5:14, 15) Mkhristu amene amatengeka ndi zilakolako zoipa mpaka kufika pochita tchimo lalikulu, amakhala kuti akudwala mwauzimu. Apa tikutanthauza kuti munthuyo salinso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndiyeno akulu amakhala ngati madokotala amene amayesetsa ‘kuchiritsa wodwalayo.’ Ngati munthuyo walapa kuchokera mumtima, malangizo awo ochokera m’Malemba angamuthandize kuti akonze ubwenzi wake ndi Mulungu.—Mac. 3:19; 2 Akor. 2:5-10. w19.05 10 ¶10-11
Lachitatu, August 4
Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.
Yehova angatipatse mtima wofuna kuchita zinthu zinazake. Mwina tikhoza kumva kuti pali zinthu zina zimene zikufunika mumpingo kapena kwina. Ndiye mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndingathandize bwanji?’ Kapena mwina tingapatsidwe utumiki wovuta n’kumakayikira ngati tingauchite bwino. Mwinanso pambuyo powerenga mavesi ena a m’Baibulo tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mavesiwa pothandiza ena?’ Yehova akaona kuti tikuganizira zoti tichite zinazake, iye angatipatse mtima wofuna kuchita zomwe tikuganizazo. Yehova angatipatsenso mphamvu zochitira zinthu zimene amafuna. (Yes. 40:29) Iye angagwiritse ntchito mzimu woyera kuti awonjezere luso limene tili nalo kale. (Eks. 35:30-35) Yehova angagwiritsenso ntchito gulu lake kutiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito inayake. Ngati simukudziwa mmene mungagwirire ntchito imene mwapatsidwa, muzipempha ena kuti akuthandizeni. Komanso muzipempha Atate wathu wakumwamba kuti akupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akor. 4:7; Luka 11:13. w19.10 21 ¶3-4
Lachinayi, August 5
Anthu adzakhala odzikonda.—2 Tim. 3:2.
Dzikoli limalimbikitsa anthu kuti azidziona kuti ndi ofunika kwambiri. Buku lina linanena kuti zaka za m’ma 1970, “mabuku opereka malangizo kwa anthu okhudza mmene angakhalire ndi moyo wabwino anachuluka kwambiri.” Mabuku ena “ankalimbikitsa anthu kuti ayenera kudzidziwa bwino ndipo ayenera kumasangalala ndi mmene alili basi.” Mwachitsanzo, m’buku lina analembamo kuti: “Uzidzikonda wekha chifukwa ngati pali munthu wooneka bwino, wofunika komanso wosangalatsa ndi iweyo basi.” Bukulo linkalimbikitsa anthu kuti “aziyendera mfundo zimene iwowo aona kuti ndi zabwino kapena zothandiza.” Kodi munamvapo maganizo ngati amenewa? Satana analimbikitsa Hava kuchita zinthu ngati zimenezi. Iye anamuuza kuti ‘adzafanana ndi Mulungu ndipo adzadziwa zabwino ndi zoipa.’ (Gen. 3:5) Masiku ano, anthu ambiri ndi onyada kwambiri moti amaona kuti munthu wina, ngakhalenso Mulungu, sangawauze kuti izi n’zoyenera, izi n’zosayenera. Zimenezi zimaonekera kwambiri m’maganizo a anthu pa nkhani ya ukwati. w19.05 23 ¶10-11
Lachisanu, August 6
Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa. Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.—Sal. 38:6.
Mfumu Davide nthawi zina ankavutika ndi nkhawa. Tangoganizirani mavuto ena amene anakumana nawo. Iye ankadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zinthu zolakwika zimene anachita. (Sal. 40:12) Mwana wake Abisalomu anamuukira kenako anaphedwa. (2 Sam. 15:13, 14; 18:33) Ndipo mnzake wapamtima anamuchitira chiwembu. (2 Sam. 16:23–17:2; Sal. 55:12-14) Masalimo ambiri amene Davide analemba amasonyeza kuti ankakhumudwa koma ankadalira kwambiri Yehova. (Sal. 38:5-10; 94:17-19) Munthu winanso amene analemba masalimo anayamba kusirira moyo wa anthu ochita zoipa. N’kutheka kuti munthu ameneyu anali wa m’banja la Asafu ndipo ankatumikira “m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.” Munthuyu anada nkhawa kwambiri moti sankasangalala ndipo ankaona kuti zinthu sizikumuyendera. Iye anafika poganiza kuti madalitso amene Yehova amapereka si okwanira.—Sal. 73:2-5, 7, 12-14, 16, 17, 21. w19.06 17 ¶12-13
Loweruka, August 7
Tikudziwa bwino ziwembu [za Satana].—2 Akor. 2:11.
Satana amakopa anthu ndi zinthu zimene aliyense amalakalaka. Mwachibadwa, anthufe timalakalaka kuphunzira zinthu zimene zingatithandize kupeza zofunika pa moyo wathu komanso wa banja lathu. (1 Tim. 5:8) Kuti tiphunzire zinthu zimenezi, timafunika kupita kusukulu komanso kulimbikira maphunziro. Koma tiyenera kusamala pa nkhani imeneyi. M’mayiko ambiri, masukulu amaphunzitsa anthu luso la ntchito komanso nzeru za anthu. Zimene anthu amaphunzitsidwa zimawachititsa kukayikira zoti kuli Mulungu komanso kuti asamatsatire mfundo za m’Baibulo. Amaphunzitsidwa kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. (Aroma 1:21-23) Mfundo zimenezi n’zosemphana kwambiri ndi nzeru yochokera kwa Mulungu. (1 Akor. 1:19-21; 3:18-20)Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti tipewe kutsatira “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake” zimene zimapezeka m’dziko la Satanali. (Akol. 2:8) Nthawi zonse tizikhala osamala kuti Satana asatigwire ngati nyama. (1 Akor. 3:18) Tisalole kuti atichititse kuona Yehova molakwika. Nthawi zonse tizitsatira mfundo zapamwamba za Yehova. Ndipo tisalole kuti Satana atipusitse n’kusiya kutsatira malangizo a Mulungu. w19.06 5 ¶13; 7 ¶17
Lamlungu, August 8
[Muziwaphunzitsa] kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.—Mat. 28:20.
Kaya musankha nkhani yotani, chofunika ndi kuganizira za anthu amene mungakumane nawo. Muziganizira mmene mfundo za m’Baibulo zingawathandizire. Mukamakambirana nawo, muzimvetsera zimene akunena komanso kulemekeza maganizo awo. Mukamatero mukhoza kuwamvetsa bwino ndipo iwonso angamvetsere uthenga umene mwawatengera. Munthu asanayambe kuphunzira Baibulo, timafunika kuchita maulendo obwereza angapo. Tikutero chifukwa chakuti nthawi zambiri, anthu sapezeka tikapita kukachita ulendo wobwereza. Nthawi zina pangafunikenso kuchita maulendo obwereza angapo kuti munthu afike pomasuka nafe n’kuyamba kuphunzira. Tiyenera kukumbukira kuti maluwa amakula akamathiriridwa pafupipafupi. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene timakambirana naye Baibulo. Iye akhoza kuyamba kukonda kwambiri Yehova komanso Yesu tikamakambirana naye Mawu a Mulungu pafupipafupi. w19.07 14 ¶1; 15-16 ¶7-8
Lolemba, August 9
Ndinu odala anthu akamadana nanu, kukusalani, kukunyozani ndi kukana dzina lanu n’kumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu.—Luka 6:22.
Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamenepa? Iye sankatanthauza kuti Akhristu azisangalala akamadedwa. Koma ankangofotokoza mmene zinthu zizikhalira. Akhristufe sitili mbali ya dziko. Timatsatira mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo timalalikira uthenga umene iye ankalalikira. Izi zimachititsa kuti anthu m’dzikoli azidana nafe. (Yoh. 15:18-21) Koma chomwe ife timafuna n’kusangalatsa Yehova basi. Ndiye kaya anthu ena azidana nafe chifukwa choti timakonda Atate athu, zimenezo ndi zawo. Koma sitiyenera kuganiza kuti ndife opanda pake ngati anthu ena sasangalala nafe. Sitikudziwa kuti ndi liti pamene tingazunzidwe kapena kuletsedwa kulambira Yehova. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti tikhoza kukonzekera panopa. Tingakonzekere polimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova, kuyesetsa kuti tikhale olimba mtima komanso kudziwa zochita ngati anthu akudana nafe. Kukonzekera panopa kungatithandize kuti tisadzasiye kutumikira Yehova m’tsogolo. w19.07 6 ¶17-18; 7 ¶21
Lachiwiri, August 10
Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi.—Aheb. 11:6.
Tikamaphunzira ndi anthu amene sakonda zachipembedzo tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti azikhulupirira zoti kuli Mulungu. Tiziwathandizanso kuti azikhulupirira Baibulo. Mwina tingafunike kubwereza mfundo zina maulendo angapo. Mwina ulendo uliwonse umene tikuphunzira tiyenera kukambirana nawo umboni wakuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Tingawasonyeze kuti maulosi ake amakwaniritsidwa, ndi lolondola pa nkhani za sayansi komanso mbiri yakale kapena umboni wakuti lili ndi mfundo zothandiza pa moyo wathu. Kuti tithandize anthu kukhala ophunzira a Khristu, tiyenera kuwasonyeza chikondi mosaganizira kuti ali ndi chipembedzo kapena ayi. (1 Akor. 13:1) Cholinga chathu pophunzira nawo chizikhala chowathandiza kudziwa kuti Mulungu amatikonda ndipo amafuna kuti ifenso tizimukonda. Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri amene sankakonda zopembedza amabatizidwa chifukwa choti ayamba kukonda Mulungu. Choncho tiyeni tizikhala ndi maganizo oyenera ndipo tizisonyeza chikondi kwa anthu a mitundu yonse. Tizimvetsera zimene akulankhula n’kumvetsa maganizo awo. Tiziwapatsanso chitsanzo chabwino chimene chingawathandize kukhala ophunzira a Khristu. w19.07 24 ¶16-17
Lachitatu, August 11
Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.—Aheb. 13:16.
Ana aakazi a Salumu anathandiza nawo pa ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:20; 3:12) Ngakhale kuti bambo awo anali kalonga, iwo anadzipereka kugwira nawo ntchito yovuta komanso yoopsa imeneyi. (Neh. 4:15-18) Masiku anonso, alongo ena amadzipereka kuti atumikire Yehova pa ntchito zomangamanga kapena kukonza malo amene anaperekedwa kwa Yehova. Luso lawo, khama lawo komanso kukhulupirika kwawo zimathandiza kwambiri kuti ntchitozi ziziyenda bwino. Yehova analimbikitsanso Tabita kuti azigwira “ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo” makamaka pothandiza akazi amasiye. (Mac. 9:36) Popeza anali wokoma mtima komanso wopatsa, anthu ambiri analira atamwalira. Koma anasangalala kwambiri Petulo atamuukitsa. (Mac. 9:39-41) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Tabita? Kaya ndife aang’ono kapena achikulire, amuna kapena akazi, tonse tikhoza kuchita zinthu zina pothandiza abale ndi alongo athu. w19.10 23 ¶11-12
Lachinayi, August 12
Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, kuti mukhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena.—Afil. 1:10.
Kodi tingakhumudwitse bwanji munthu? Taganizirani chitsanzo ichi. Tiyerekeze kuti munthu wina anali chidakwa ndiye pambuyo pophunzira Baibulo anayesetsa kwa nthawi yaitali kuti azidziletsa. Kenako anazindikira kuti ayenera kungosiyiratu mowa ndipo anabatizidwa. Ndiye tsiku lina waitanidwa kuti akacheze ndi abale ndi alongo ndipo amene wamuitanayo akumupatsa mowa n’kunena kuti: “Aaa imwani. Panotu ndinu Mkhristu ndipo mukutsogoleredwa ndi mzimu woyera. Paja khalidwe lina limene mzimu umatulutsa ndi kudziletsa. Ndipo ngati ndinu odziletsa sizingakuvuteni kudziwa malire omwera mowawu.” Kodi mukuganiza kuti chingachitike n’chiyani ngati m’bale watsopanoyu atatsatira malangizo olakwikawa? Misonkhano yathu imatithandiza kutsatira malangizo a mulemba la lero. Imatithandiza kukumbukira zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zofunika kwambiri komanso mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zomwe timaphunzira n’cholinga choti tikhale opanda cholakwa. Imatilimbikitsanso kuti tizikonda Mulungu komanso Akhristu anzathu. Ndipo kukonda Mulungu ndi anzathu kuchokera mumtima kungatithandize kuti tiziyesetsa kuti tisakhumudwitse abale athu. w19.08 10 ¶9; 11 ¶13-14
Lachisanu, August 13
Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.—1 Akor. 15:9.
Sikuti anthu onse amene amaoneka omasuka kwambiri kapena osadzikayikira ndi odzikuza. (Yoh. 1:46, 47) Koma kaya ndife omasuka kapena ayi, tonsefe tiyenera kuyesetsa kukhala ndi mtima wodzichepetsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri pokhazikitsa mipingo m’mizinda yosiyanasiyana. N’kutheka kuti iye anachita zambiri mu utumiki kuposa atumwi ena onse a Yesu Khristu. Koma Paulo sankadziona ngati wapamwamba. Iye ananena kuti anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulunguyo osati chifukwa cha makhalidwe ake kapena ntchito zake. (1 Akor. 15:10) Kalata ya Paulo yopita kwa Akorinto imasonyeza kuti iye anali wodzichepetsa kwambiri. Izi zimaonekera bwino tikaganizira zoti sankalimbana ndi anthu ena mumpingowo amene ankapikisana naye.—2 Akor. 10:10. w19.09 3 ¶5-6
Loweruka, August 14
Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?—Aheb. 12:9.
Chifukwa chimodzi chimene chimachititsa kuti tizivutika kumvera Yehova n’chakuti si ife angwiro. Choncho nthawi zina sitifuna kumvera Mulungu. Pamene Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Yehova n’kudya chipatso choletsedwa, anasonyeza kuti akufuna kumasankha okha chabwino ndi choipa. (Gen. 3:22) Masiku anonso, anthu ambiri samvera Yehova ndipo amasankha okha kuti izi n’zoyenera, izi n’zosayenera. Ngakhale anthu amene amadziwa Yehova komanso kumukonda angavutike kumugonjera pa zinthu zina. Nayenso mtumwi Paulo ankavutika. (Aroma 7:21-23) Mofanana ndi Paulo, timafuna kuchita zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zabwino. Koma nthawi zonse tiyenera kuyesetsa kudziletsa kuti tisachite zoipa. Tingavutikenso kugonjera Yehova chifukwa chakuti timasokonezedwa ndi chikhalidwe cha kumene tinakulira. Maganizo a anthu ambiri amasiyana ndi maganizo a Yehova choncho tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tisamatengere maganizo a anthuwo. w19.09 15 ¶4-6
Lamlungu, August 15
Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. . . . Ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.—Maliko 10:21.
Tiyenera kuzindikira kuti mphamvu zathu zili ndi malire. Choncho tizisamala kuti tisamachite zinthu zambiri kuposa zimene tingakwanitse. Mwachitsanzo, tikhoza kumatanganidwa kwambiri poyesetsa kupeza chuma. Koma ndi bwino kukumbukira zimene Yesu anauza mnyamata wina wachuma amene anamufunsa kuti: “Ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?” Mnyamatayo ayenera kuti anali munthu wabwino. Tikutero chifukwa chakuti buku la Maliko limanena kuti Yesu “anam’konda.” Yesu anauza mnyamatayo mawu ali pamwambawa. Munthuyo ankafuna kuchita zimene Yesu ananenazi koma zikuoneka kuti sankafuna kuluza ‘katundu wake wambiri.’ (Maliko 10:17-22) Choncho anakana goli la Yesu ndipo anapitiriza kukhala kapolo wa “Chuma.” (Mat. 6:24) Kodi mukanakhala inuyo mukanatani? Nthawi zina tiyenera kudzifufuza kuti tidziwe zimene tikuika pamalo oyamba. Zimenezi zingatithandize kutsimikizira kuti tikugwiritsa ntchito mwanzeru mphamvu zathu. w19.09 24 ¶17-18
Lolemba, August 16
M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe choyamba.—Maliko 13:10.
Ntchito yathu yolalikira idzatha pokhapokha Yehova atanena kuti tamaliza. Sitikudziwa kuti kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti anthu aphunzire za Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. (Yoh. 17:3) Koma chomwe tikudziwa n’chakuti anthu a “maganizo abwino” adakali ndi mwayi womvetsera uthenga wabwino mpaka pamene chisautso chachikulu chidzayambe. (Mac. 13:48) Ndiye kodi tingathandize bwanji anthu amenewa? Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake kuti azitipatsa zinthu zonse zofunika kuti tiziphunzitsa choonadi. Mwachitsanzo, timaphunzira zambiri pamsonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Timaphunzira zimene tinganene mu utumiki pa ulendo woyamba komanso wobwereza. Ngati mutasiyira munthu amene wasonyeza chidwi kapepala kapena magazini, akhoza kupitiriza kuwerenga mpaka pa nthawi imene mudzakumane nayenso. Ndi udindo wa Mkhristu aliyense kuti azichita zonse zimene angathe polalikira mwezi uliwonse. w19.10 9 ¶7; 10 ¶9-10
Lachiwiri, August 17
Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.—Aheb. 13:16.
Yehova analonjeza Simiyoni, yemwe anali bambo wachikulire ku Yerusalemu, kuti sadzamwalira asanaone Mesiya. Simiyoni ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi lonjezoli chifukwa anali atadikira kwa zaka zambiri kuti Mesiya afike. Iye anadalitsidwa chifukwa chopirira komanso kukhala ndi chikhulupiriro. Tsiku lina, Simiyoni analowa m’kachisi “motsogoleredwa ndi mzimu.” Atalowa anaona Yesu ndipo Yehova anagwiritsa ntchito Simiyoniyo kuti anene ulosi wokhudza mwanayo, yemwe anadzakhala Khristu. (Luka 2:25-35) Simiyoni ayenera kuti anamwalira Yesu asanayambe utumiki wake padzikoli, koma iye anayamikira mwayi wakewu ndipo adzadalitsidwa kwambiri m’tsogolo. M’dziko latsopano, munthu wokhulupirikayu adzaona madalitso amene anthu onse padzikoli adzapeza chifukwa cha ulamuliro wa Yesu. (Gen. 22:18) Nafenso tiyenera kuyamikira mwayi uliwonse umene timakhala nawo potumikira Yehova. w19.10 22 ¶7; 23 ¶12
Lachitatu, August 18
Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa.—Miy. 4:23.
Tonsefe tiyenera kuteteza mtima wathu, kaya tili ndi ndalama zambiri kapena zochepa. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kupewa kukonda chuma. Komanso tisamalole kuti ntchito yathu ikhale pamalo oyamba m’malo mwa kutumikira Yehova. Koma kodi mungadziwe bwanji ngati mwayamba kukonda chuma? Mukhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakonda kuganizira za ntchito yanga ndikakhala kumisonkhano kapena mu utumiki? Kodi ndimadera nkhawa kwambiri kuti mwina sindidzakhala ndi ndalama zokwanira m’tsogolo? Kodi nkhani za ndalama komanso chuma zimayambitsa mavuto m’banja lathu? Kodi ndingalolere kugwira ntchito imene anthu ena amainyoza ngati ingandithandize kuchita zambiri potumikira Yehova?’ (1 Tim. 6:9-12) Tikamaganizira mafunso amenewa, tizikumbukira kuti Yehova amatikonda komanso analonjeza anthu odzipereka kwa iye kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama.”—Aheb. 13:5, 6. w19.10 29 ¶10
Lachinayi, August 19
Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.—Miy. 27:17.
Tikamagwira ntchito limodzi ndi Akhristu anzathu, timaona makhalidwe awo abwino, timaphunzira zinthu zina komanso timayamba kugwirizana nawo kwambiri. Mwachitsanzo, kodi mumamva bwanji mukaona mnzanu mu utumiki akulankhula molimba mtima za chikhulupiriro chake komanso zokhudza Yehova ndi zolinga zake? Mungafune kuti muzigwirizana naye kwambiri. Mlongo wina wazaka 23 dzina lake Adeline anapempha mnzake dzina lake Candice kuti akalalikire limodzi m’gawo limene sililalikidwa kawirikawiri. Iye ananena kuti: “Tinkaona kuti zimenezi zikhoza kutilimbikitsa mwauzimu komanso kutithandiza kuti tizikonda kwambiri utumiki.” Kodi kugwira ntchito limodzi kunawathandiza bwanji? Adeline anati: “Tikaweruka mu utumiki, tinkakambirana mmene tinkamvera, zimene zinatilimbikitsa pokambirana ndi anthu komanso mmene Yehova anatithandizira. Tonse tinkasangalala pokambirana mochokera pansi pa mtima ndipo zinkatithandiza kuti tidziwane bwino kwambiri.” w19.11 5 ¶10-11
Lachisanu, August 20
Nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro.—Aef. 6:16.
Kale, msilikali ankachita manyazi akabwera kunkhondo wopanda chishango chake. Wolemba mbiri yakale wa ku Rome dzina lake Tacitus, ananena kuti: “Msilikali akabwera kunkhondo wopanda chishango chake ankanyozeka kwambiri.” Ichi ndi chifukwa chimodzi chimene asilikali ankagwirira mwamphamvu zishango zawo. Timagwira mwamphamvu chishango chathu chachikhulupiriro tikamapezeka pamisonkhano yathu nthawi zonse komanso kuuza ena za dzina la Yehova ndi Ufumu wake. (Aheb. 10:23-25) Tiyeneranso kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse n’kumapempha Yehova kuti atithandize kutsatira malangizo ake pa zonse zimene timachita. (2 Tim. 3:16, 17) Tikamatero, chida chilichonse chimene Satana angagwiritse ntchito sichidzativulaza mpaka kalekale. (Yes. 54:17) ‘Chishango chathu chachikulu chachikhulupiriro’ chidzatiteteza ndipo tidzakhala olimba mtima n’kumatumikira mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Tikamachita zimenezi, chikhulupiriro chathu chidzakhalabe cholimba ndipo tidzakhala ndi mwayi wokhala kumbali ya Yesu akadzapambana pa nkhondo yolimbana ndi Satana limodzi ndi gulu lake.—Chiv. 17:14; 20:10. w19.11 19 ¶18-19
Loweruka, August 21
Mmene ndikuponyera nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi.—1 Akor. 9:26.
Kulemba pulani yanu yochitira zinthu kungakuthandizeni kuti mukwaniritse zimene munasankha. (1 Akor. 14:40) Mwachitsanzo, mabungwe a akulu amalimbikitsidwa kuti azisankha mkulu woti azilemba zimene bungwelo lasankha kuchita, amene asankhidwa kuti azichite komanso nthawi imene ayenera kumaliza zinthuzo. Akulu amene amatsatira malangizowa amakwaniritsa zimene asankha mosavuta. Zimenezi zingakuthandizeninso kukwaniritsa zomwe munasankha. Mwachitsanzo, mukhoza kulemba zinthu zimene mukufunika kuchita tsiku lililonse n’kusonyeza zimene muziyambira kuchita ndi zimene muzimalizira. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mumalize zimene munayamba kuchita komanso kuti muchite zinthu zambiri pa nthawi yochepa. Koma muyenera kuchita khama. Pamafunika khama kuti mutsatire pulani yanu komanso mumalize zimene munayamba. (Aroma 12:11) Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti ‘apitirize kukhala wodzipereka’ n’kumayesetsa kukhala mphunzitsi wabwino. Malangizowa angatithandizenso kuti tizikwaniritsa zolinga zina zauzimu.—1 Tim. 4:13, 16. w19.11 29-30 ¶15-16
Lamlungu, August 22
Yehova anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso, mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake.—Eks. 33:11.
Mose atauzidwa kuti atsogolere Aisiraeli pochoka ku ukapolo, ankadzikayikira moti anauza Yehova mobwerezabwereza kuti sangakwanitse. Mulungu anamuchitira chifundo kwambiri, ndipo anamuthandiza. (Eks. 4:10-16) Chifukwa cha zimenezi, Mose anakwanitsa kupereka mauthenga amphamvu a chiweruzo kwa Farao. Iye anaona Yehova akugwiritsa ntchito mphamvu zake populumutsa Aisiraeli n’kuwononga Farao ndi anthu ake m’Nyanja Yofiira. (Eks. 14:26-28; Sal. 136:15) Mose atachoka ku Iguputo ndi Aisiraeli, iwo ankangokhalira kudandaula. Koma Mose anaona Yehova akuleza mtima kwambiri pochita zinthu ndi anthu amene anawamasula ku ukapolowa. (Sal. 78:40-43) Pa nthawi ina, Mose atapempha Yehova kuti asinthe maganizo ake, Iye anasonyeza kudzichepetsa n’kusintha maganizowo. (Eks. 32:9-14) Mose atachoka ku Iguputo ndi Aisiraeli, ubwenzi wake ndi Yehova unalimba kwambiri moti zinali ngati ankaona Atate wake wakumwambayo.—Aheb. 11:27. w19.12 17
Lolemba, August 23
Watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona.—Mat. 28:7.
Ophunzira ambiri a Yesu anali ochokera ku Galileya. Choncho paphiri linalake la ku Galileya panali pabwino kuchitira msonkhano wa anthu ambiri kusiyana ndi kuchitira m’nyumba ya munthu ku Yerusalemu. Komanso Yesu ataukitsidwa, anali ataonekera kale kwa atumwi ake 11 m’nyumba ina ku Yerusalemu. Ngati iye akanafuna kuuza atumwi ake okha kuti azilalikira komanso kuphunzitsa anthu, akanachita zimenezi ku Yerusalemuko. Sakanawauza kuti akakumane ku Galileya limodzi ndi azimayi aja komanso anthu ena. (Luka 24:33, 36) Yesu sanangopereka lamulo lija kwa Akhristu a m’nthawi ya atumwi okha. Tikutero chifukwa chakuti iye atapereka lamuloli, anamaliza ndi mawu akuti: “Ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Masiku ano, ntchito yophunzitsa anthu ikuyenda bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti chaka chilichonse anthu pafupifupi 300,000 amabatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu Khristu. w20.01 2 ¶1; 3 ¶5-6
Lachiwiri, August 24
Anatikumbukira pamene [tinali okhumudwa].—Sal. 136:23.
Taganizirani mavuto awa: Ndinu wachinyamata ndipo akupezani ndi matenda oopsa. Kapena ndinu wachikulire ndipo simukupeza ntchito. Apo ayi, mukulephera kuchita zambiri potumikira Yehova chifukwa cha uchikulire. Ngati mukukumana ndi mavuto ngati amene tatchulawa, mwina mungamaone kuti ndinu wopanda ntchito. Zimenezi zingachititse kuti musamasangalale, muzidziona kuti ndinu wosafunika komanso mungamavutike kugwirizana ndi anthu ena. Anthu am’dzikoli amatengera maganizo a Satana pa nkhani ya moyo wa anthu. Satana amachitira anthu zinthu ngati kuti ndi osafunika. Iye anasonyeza kuipa mtima pouza Hava kuti adzakhala pa ufulu akapanda kumvera Mulungu, chonsecho akudziwa kuti adzafa. Satana ndi amene amalamulira zinthu m’dzikoli. Choncho n’zosadabwitsa kuti atsogoleri ambiri am’dzikoli amatengera maganizo ake osalemekeza moyo komanso anthu. Koma Yehova amafuna tizidziona kuti ndife amtengo wapatali ndipo amatithandiza tikakumana ndi zinthu zimene zingatichititse kumva kuti ndife achabechabe.—Aroma 12:3. w20.01 14 ¶1-4
Lachitatu, August 25
Usanenere m’dzina la Yehova, ngati ukufuna kuti tisakuphe.—Yer. 11:21.
Kwa zaka zosachepera 40, Yeremiya ankakhala pafupi ndi anthu osakhulupirika ndipo n’kutheka kuti ena anali achibale ake ochokera kwawo ku Anatoti. (Yer. 12:6) Koma anapezabe anthu ocheza nawo. Iye ankauza mlembi wake wokhulupirika dzina lake Baruki zamumtima mwake ndipo zinalembedwa kuti ifenso tizidziwe. (Yer. 8:21; 9:1; 20:14-18; 45:1) Pamene Baruki ankalemba zimene zinkachitikira Yeremiya, anthu awiriwa ayenera kuti anayamba kukondana komanso kulemekezana kwambiri. (Yer. 20:1, 2; 26:7-11) Kwa zaka zambiri, Yeremiya ankachenjeza Aisiraeli molimba mtima zimene zidzachitikire Yerusalemu. (Yer. 25:3) Pofuna kuthandiza anthu kuti alape, Yehova anapempha Yeremiya kuti alembe machenjezowo mumpukutu. (Yer. 36:1-4) Yeremiya ndi Baruki anagwira limodzi ntchito imene Mulungu anawapatsayi ndipo n’kutheka kuti inatenga miyezi yambiri. Pa nthawiyo, ayenera kuti ankakambirana zinthu zolimbitsa chikhulupiriro chawo. w19.11 2-3 ¶3-4
Lachinayi, August 26
Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.—Mat. 23:12.
Kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi abale ndi alongo odzozedwa? Si bwino kugomera kwambiri munthu ngakhale atakhala wodzozedwa, kapena kuti m’bale wake wa Khristu. (Mat. 23:8-11) Baibulo limanena kuti tiyenera ‘kutsanzira chikhulupiriro’ cha akulu osati kuona munthu winawake ngati mtsogoleri wathu. (Aheb. 13:7) N’zoona kuti Baibulo limanena kuti anthu ena ndi oyenera kuwapatsa “ulemu waukulu.” Koma limanena kuti tizichita zimenezi chifukwa choti ‘amatsogolera bwino’ komanso “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa,” osati chifukwa choti adzozedwa. (1 Tim. 5:17) Tikamachita chidwi kwambiri ndi odzozedwa kapena kuwatamanda zikhoza kuwachititsa manyazi. Apo ayi, tikhoza kuwachititsa kuti ayambe kunyada. (Aroma 12:3) Ndiye palibe amene angafune kuchititsa abale a Yesu kuti alakwitse zinthu chonchi.—Luka 17:2. w20.01 29 ¶8
Lachisanu, August 27
Kuwonjezera pa zinthu za kunja kwa thupi zimenezo, palinso . . . nkhawa imene ndimakhala nayo pa mipingo yonse.—2 Akor. 11:28.
Panali zinthu zambiri zimene mtumwi Paulo ankada nazo nkhawa. Mavuto amene abale ndi alongo ankakumana nawo ankamudetsa nkhawa. (2 Akor. 2:4) Anthu amene ankamutsutsa pa ntchito yake yolalikira nthawi zina ankamumenya komanso kumutsekera m’ndende. Ankakumananso ndi mavuto amene ankamudetsa nkhawa monga ‘kusowa’ zinthu zina zofunika pa moyo. (Afil. 4:12) Komanso popeza chombo chinamuswekerapo katatu, n’zosachita kufunsa kuti ankakhala ndi nkhawa akamayenda panyanja. (2 Akor. 11:23-27) Kodi n’chiyani chinkathandiza Paulo akakhala ndi nkhawa? Paulo ankada nkhawa ndi mavuto amene abale ndi alongo ake ankakumana nawo, koma sankalimbana ndi mavuto onsewo payekha. Iye ankadziwa kuti sangakwanitse kuchita zimenezi. Choncho anakonza zoti abale ena okhulupirika monga Timoteyo ndi Tito azithandiza posamalira mipingo. N’zodziwikiratu kuti ntchito imene abalewa ankagwira inathandiza kuti Paulo asamade nkhawa kwambiri.—Afil. 2:19, 20; Tito 1:1, 4, 5. w20.02 23 ¶11-12
Loweruka, August 28
Ananu, muzimvera makolo anu.—Aef. 6:1.
Yehova amafuna kuti ana azimvera makolo awo ndipo amafunanso kuti ifeyo tizimumvera iyeyo. Tiyenera kumumveradi chifukwa ndi amene anatilenga, ndi amene amatipatsa zofunika pa moyo komanso ndi wanzeru kuposa makolo onse. Koma chifukwa chachikulu chotilimbikitsa kumvera Yehova n’chakuti timamukonda. (1 Yoh. 5:3) Ngakhale kuti pali zifukwa zambiri zotichititsa kumumvera, iye satikakamiza kuchita zimenezi. Iye anatipatsa ufulu wosankha ndipo amasangalala tikamamumvera mwa kufuna kwathu. Makolo amafuna kuti ana awo akhale otetezeka. N’chifukwa chake amawaphunzitsa makhalidwe abwino pofuna kuwateteza. Ana akamatsatira malangizo a makolo awo amasonyeza kuti amawadalira komanso kuwalemekeza. Ngati zili choncho ndi makolo, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba? Kudziwa komanso kutsatira mfundo zake n’kofunika kwambiri. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timakonda Atate wathu komanso kumulemekeza ndipo zinthu zimatiyendera bwino. (Yes. 48:17, 18) Koma anthu amene amakana Yehova komanso mfundo zake amakumana ndi mavuto.—Agal. 6:7, 8. w20.02 9-10 ¶8-9
Lamlungu, August 29
Lolani kapolo wanu wamkazi alankhule nanu ndipo mvetserani mawu a kapolo wanu.—1 Sam. 25:24.
Mofanana ndi Abigayeli, nafenso tiyenera kulimba mtima n’kulankhula ngati taona kuti zimene munthu wina akufuna kuchita zingamubweretsere mavuto. (Sal. 141:5) Tiyenera kulankhula mwaulemu koma molimba mtima. Tikamapereka malangizo oyenera kwa munthu timasonyeza kuti ndife mnzake weniweni. (Miy. 27:17) Makamaka akulu ayenera kulimba mtima n’kulankhula ndi anthu amene ayamba kuyenda panjira yolakwika. (Agal. 6:1) Akuluwo amakumbukira kuti nawonso si angwiro ndipo nthawi zina angafunike kulangizidwa. Koma zimenezi sizingawalepheretse kuthandiza anthu amene akufunika kulangizidwa. (2 Tim. 4:2; Tito 1:9) Iwo amayesetsa kuti apereke malangizowo mwaluso komanso moleza mtima. Amachita zonsezi chifukwa chokonda m’bale wawoyo. (Miy. 13:24) Koma chofunika kwambiri kwa iwo ndi kulemekeza Yehova polimbikitsa anthu kutsatira mfundo zake komanso kuteteza mpingo kuti usasokonezedwe.—Mac. 20:28. w20.03 20 ¶8-9
Lolemba, August 30
Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.—Afil. 4:13.
Yehova anathandiza Mose kuti apulumutse Aisiraeli. Koma kodi anamugwiritsa ntchito pa nthawi iti? Kodi ndi pa nthawi imene Mose ankaona kuti angagwire bwino ntchitoyi pambuyo ‘pophunzira nzeru zonse za Aiguputo’? (Mac. 7:22-25) Ayi, koma Yehova anamugwiritsa ntchito atamuphunzitsa kuti akhale wodzichepetsa komanso wofatsa. (Mac. 7:30, 34-36) Yehova anathandiza Mose kuti alimbe mtima n’kukalankhula ndi wolamulira wamphamvu kwambiri wa ku Iguputo. (Eks. 9:13-19) Yehova amagwiritsa ntchito anthu amene amatsanzira makhalidwe ake komanso kumudalira. Kuyambira kale, Yehova wakhala akuthandiza atumiki ake kuti azichita zinthu zosiyanasiyana. Nanga kodi inuyo adzakuthandizani kuchita chiyani? Yankho lake lingadalire zimene inuyo mungadzipereke kuchita. (Akol. 1:29) Mukadzipereka, Yehova angakuthandizeni kukhala munthu wolalikira mwakhama, wophunzitsa mwaluso, wotonthoza ena, wogwira ntchito mwaluso, wothandiza ena kapenanso wochita chilichonse chimene iye akufuna kuti akwaniritse cholinga chake. w19.10 21 ¶5; 25 ¶14
Lachiwiri, August 31
Ndakutchani mabwenzi.—Yoh. 15:15.
Anzathu abwino amatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova. Kuti tipeze anzathu abwino, ifenso tiyenera kukhala aubwenzi. (Mat. 7:12) Mwachitsanzo, Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kuthandiza anzathu, makamaka amene akumana ndi mavuto. (Aef. 4:28) Tikamatanganidwa ndi kuthandiza ena timakhala osangalala kwambiri. (Mac. 20:35) Tikakhala ndi anzathu abwino, akhoza kutithandiza tikakumana ndi mavuto ndipo zimenezi zingachititse kuti tikhale ndi mtendere mumtima. Mofanana ndi Elihu amene anamvetsera Yobu akufotokoza mavuto ake, anzathu akhozanso kumvetsera moleza mtima tikamafotokoza mavuto athu. (Yobu 32:4) N’zoona kuti anzathu sangatisankhire zochita koma ndi bwino kumvetsera malangizo awo ochokera m’Malemba. (Miy. 15:22) Davide atakumana ndi mavuto analola kuthandizidwa ndi anzake. Nafenso sitiyenera kukhala odzikuza moti n’kulephera kulola kuti anzathu atithandize pa mavuto athu. (2 Sam. 17:27-29) Anzathu oterowo ali ngati mphatso yochokera kwa Yehova.—Yak. 1:17. w19.04 11 ¶12; 12 ¶14-15