September
Lachitatu, September 1
Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.—Yoh. 5:17.
Kodi khama la Yehova ndi Yesu pogwira ntchito likusonyeza kuti kupuma si kofunika? Ayi. Yehova satopa, choncho safunika kupuma. Komabe Baibulo limanena kuti Yehova atalenga kumwamba ndi dziko lapansi, “anapuma pa ntchito yake.” (Eks. 31:17) Apa zikuoneka kuti Yehova anaima kaye n’kumasangalala ndi ntchito imene anagwira. Nayenso Yesu ankagwira ntchito mwakhama ali padzikoli koma ankakhala ndi nthawi yopuma komanso kudya ndi anzake. (Mat. 14:13; Luka 7:34) Baibulo limalimbikitsa anthu a Mulungu kuti azikonda kugwira ntchito. Atumiki a Mulungu amafunika kukhala akhama osati aulesi. (Miy. 15:19) Mwina mumagwira ntchito kuti muzisamalira banja lanu. Ndipo ophunzira onse a Khristu ali ndi udindo wogwira ntchito yolalikira uthenga wabwino. Koma muyeneranso kupuma mokwanira. w19.12 2 ¶2; 3 ¶4-5
Lachinayi, September 2
Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.—1 Pet. 2:21.
Tizipewa kufotokoza nkhani zokhudza ziwanda. Tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani imeneyi. Iye asanabwere padzikoli anali kumwamba ndipo amadziwa zambiri zokhudza Satana ndi ziwanda zake. Koma sankakamba zimene mizimu yoipayi yachita. Yesu ankafuna kukhala mboni ya Yehova osati mneneri wa Satana. Ifenso tizimutsanzira popewa kufalitsa nkhani zokhudza ziwanda. M’malomwake, zolankhula zathu zizisonyeza kuti mtima wathu ‘wagalamuka ndi nkhani yosangalatsa’ yomwe ndi mfundo za choonadi. (Sal. 45:1) Tisamaope mizimu yoipa. M’dzikoli zinthu zoipa zikhoza kutichitikira. Mwachitsanzo, tingakumane ndi ngozi, matenda kapena imfa yadzidzidzi. Koma tisamaganize kuti mizimu yoipa ndi imene yachititsa. Baibulo limanena kuti “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera” aliyense. (Mlal. 9:11) Yehova wasonyeza kale kuti ndi wamphamvu kuposa ziwanda. w19.04 23-24 ¶13-14
Lachisanu, September 3
Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.—Aroma 13:1.
Kodi akulu ayenera kutsatira lamulo lokanena ku boma ngati wina akuganiziridwa kuti wagwirira mwana? Inde. M’mayiko kumene kuli lamulo loti anthu azikanena ku boma ngati wina akuganiziridwa kuti wagwirira mwana, akulu amayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi lamuloli. Zili choncho chifukwa malamulo ngati amenewa sasemphana ndi malamulo a Mulungu. (Mac. 5:28, 29) Choncho akulu akangomva kuti munthu wina wagwirira mwana, amapempha malangizo ku ofesi ya nthambi n’cholinga choti achite zinthu mogwirizana ndi malamulo a boma. Akulu amauzanso ana amene agwiriridwa, makolo awo kapena anthu ena amene akudziwa za nkhaniyi kuti akhoza kukanena nkhaniyo ku boma. Koma tiyerekeze kuti munthu amene akuganiziridwa kuti wagwirira mwana ndi wamumpingo. Ndiyeno Mkhristu wina anakanena nkhaniyo ku boma ndipo zachititsa kuti anthu ambiri a m’deralo aidziwe. Kodi Mkhristu ameneyu ayenera kuganiza kuti waipitsa dzina la Mulungu? Ayi. Zili choncho chifukwa chakuti wogwirirayo ndi amene waipitsa dzina la Mulungu. w19.05 10 ¶13-14
Loweruka, September 4
Kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa.—1 Akor. 3:19.
Baibulo limalangiza mwamuna ndi mkazi wake kuti azilemekezana komanso kukwaniritsa zimene analonjeza pa tsiku la ukwati wawo. Limalimbikitsa anthu okwatirana kuti apitirize kukhala okhulupirika m’banja mwawo. Paja Baibulo limanena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Koma mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amayendera nzeru za m’dzikoli amaona kuti mwamuna kapena mkazi ayenera kumangoganizira zofuna zake. Buku lina lofotokoza zokhudza kuthetsa banja linanena kuti: “Anthu ambiri anasintha malumbiro a ukwati. M’malo molumbira kuti tikhala m’banja ‘pa nthawi yonse imene awirife tidzakhala ndi moyo,’ amangonena kuti tikhala m’banja ‘pa nthawi yonse imene awirife tidzakhala tikukondana.’” Maganizo olakwikawa achititsa kuti mabanja ambiri azitha ndipo zotsatira zake zimakhala zopweteka kwambiri. Apa n’zoonekeratu kuti maganizo osalemekeza ukwati amene anthu a m’dzikoli ali nawo ndi opusa kwambiri. w19.05 23 ¶12
Lamlungu, September 5
Musamatengere nzeru za nthawi ino.—Aroma 12:2.
Paulo anali ndi nkhawa chifukwa zikuoneka kuti Akhristu ena ankatengera maganizo komanso nzeru zosathandiza zam’dziko la Satanali. (Aef. 4:17-19) Zimenezi zikhoza kutichitikiranso ifeyo. Satana, yemwe ndi Mulungu wa nthawi ino, ali ndi zinthu zambiri zimene amagwiritsa ntchito pofuna kuti tisiye kutumikira Yehova. Mwachitsanzo, iye akhoza kupezerapo mwayi ngati tili ndi kamtima kodziona kuti ndife ofunika kwambiri. Akhozanso kugwiritsa ntchito zinthu zina zokhudza kumene tinakulira, chikhalidwe chathu kapena maphunziro athu kuti tiziyendera maganizo ake. Koma kodi n’zotheka kuchotsa ‘zinthu zimene zinazikika molimba’ m’maganizo athu? (2 Akor. 10:4) Inde n’zotheka chifukwa Paulo analemba kuti: “Tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu, ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvera Khristu.” (2 Akor. 10:5) Yehova akhoza kutithandiza kuchita zimenezi. w19.06 8 ¶1-3
Lolemba, September 6
Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.—Sal. 73:28.
Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, Hana, Davide ndi munthu wina amene analemba masalimo ankadalira kwambiri Yehova. Iwo ankapemphera kwa iye n’kumuuza zimene zikuwadetsa nkhawa. Ankamufotokozera momasuka zimene zikuwavutitsa maganizo. Ndipo sanasiye kupita kumalo olambirira Yehova. (1 Sam. 1:9, 10; Sal. 55:22; 73:17; 122:1) Yehova anawamvera chisoni ndipo anayankha mapemphero awo. Mwachitsanzo, Hana anapeza mtendere wamumtima. (1 Sam. 1:18) Davide analemba kuti: “Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.” (Sal. 34:19) Wolemba masalimo wina uja anafika poona kuti Yehova ‘wagwira dzanja lake lamanja’ ndipo akumupatsa malangizo othandiza. (Sal. 73:23, 24) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani zimenezi? Nthawi zina tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu amene angatidetse nkhawa, koma tikhoza kuwapirira. Chongofunika ndi kuganizira mmene Yehova anathandizira anthu ena, kumudalira, kupemphera kwa iye komanso kuchita zonse zimene amatiuza.—Sal. 143:1, 4-8. w19.06 17 ¶14-15
Lachiwiri, September 7
Ngakhale mutavutika chifukwa cha chilungamo, mudzakhalabe odala.—1 Pet. 3:14.
Tisalole kuti zolankhula kapena zochita za anthu zitisokoneze mpaka kufika pochita manyazi kuti ndife a Mboni za Yehova. (Mika 4:5) Kuganizira zimene atumwi anachita ku Yerusalemu pambuyo poti Yesu waphedwa kungatithandize kuti tisamaope anthu. Iwo ankadziwa kuti atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda ankadana nawo kwambiri. (Mac. 5:17, 18, 27, 28) Koma tsiku lililonse ankapita kukachisi ndipo ankasonyeza kuti ndi otsatira a Yesu. (Mac. 5:42) Iwo sanafooke chifukwa cha mantha. Kuti nafenso tikhale opanda mantha, tiyenera kusonyeza kuti ndife a Mboni za Yehova, kaya tili kuntchito, kusukulu kapena m’dera limene timakhala. (Mac. 4:29; Aroma 1:16) N’chifukwa chiyani atumwi ankasangalala? Iwo ankadziwa chimene chinkachititsa kuti anthu azidana nawo. Ndipo ankaona kuti ndi mwayi waukulu kuzunzidwa chifukwa chochita zimene Yehova amafuna. (Luka 6:23; Mac. 5:41; 1 Pet. 2:19-21) Tikazindikira kuti anthu akudana nafe chifukwa chakuti tikuchita zinthu zoyenera, sitidzalola kuti tifooke chifukwa choopa anthuwo. w19.07 7 ¶19-20
Lachitatu, September 8
N’kololeka inde kuchita chinthu chabwino pa tsiku la sabata.—Mat. 12:12.
Yesu ndi otsatira ake a Chiyuda ankasunga Sabata chifukwa choti ankatsatira Chilamulo cha Mose. Koma zolankhula ndi zochita za Yesu zinasonyeza maganizo oyenera pa nkhani ya Sabata. Iye anasonyeza kuti kuchita zinthu zothandiza anthu ena patsikuli n’kololeka. (Mat. 12:9-11) Iye ankaona kuti kukomera anthu mtima komanso kuwathandiza pa tsikuli si kuphwanya malamulo. Zimene Yesu ankachita pa Sabata zinasonyeza chinthu chofunika chokhudza tsikuli. Popeza anthu a Mulungu ankapuma pa ntchito zawo, ankakhala ndi mwayi wochita zinthu zokhudza kulambira. Yesu anakulira m’banja limene liyenera kuti linkachita zinthu zokhudza kulambira pa tsiku la Sabata. Umboni wake ndi zimene Baibulo limanena pofotokoza za Yesu ali kwawo ku Nazareti. Limanena kuti: “Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, [Yesu] analowa m’sunagoge, ndi kuimirira kuti awerenge Malemba.” (Luka 4:15-19) Ophunzira ake nawonso ankalemekeza kwambiri lamulo la Sabata moti anasiya kupanga zonunkhiritsa zoti akonzere thupi la Yesu mpaka tsiku la Sabata litadutsa.—Luka 23:55, 56. w19.12 4 ¶10
Lachinayi, September 9
Munalibe chiyembekezo.—Aef. 2:12.
Mkhristu aliyense amathandiza pofufuza anthu amtima wabwino. Tingayerekezere ntchitoyi ndi kufufuza mwana amene wasowa. Pa nthawi ina, mnyamata wazaka zitatu anasowa ndipo anthu 500 anathandiza pomufufuza. Patapita maola 20, munthu wina anamupeza m’munda wachimanga. Koma munthuyo anakana kuti ayamikiridwe ndipo anati: “Pali anthu mahandiredi angapo amene anagwira ntchito yofufuza mwanayu.” Anthu ambiri ali ngati mwana amene anasowayu chifukwa chakuti amamva ngati asochera. Iwo alibe chiyembekezo chilichonse koma amafuna kuthandizidwa. Anthu oposa 8 miliyoni akuyesetsa kupeza anthu amtima wabwino. Mwina inuyo simunapeze munthu woti muphunzire naye Baibulo. Koma ofalitsa ena omwe amayendanso m’gawo lanu akhoza kupeza munthu amene akufuna kuphunzira. M’bale kapena mlongo akapeza munthu n’kufika pokhala wophunzira wa Khristu, aliyense amene anathandiza pofufuza anthu amasangalala. w19.07 16-17 ¶9-10
Lachisanu, September 10
Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.—Afil. 3:14.
Mtumwi Paulo anawakumbutsa Akhristu a ku Filipi kuti apitirize kuthamanga pa mpikisanowo mopirira. Akhristuwo anakhala akuzunzidwa kuchokera pamene mpingowo unayamba. Mavutowo anayamba pamene Paulo ndi Sila anafika ku Filipi cha m’ma 50 C.E., atauziridwa ndi Mulungu kuti: “Wolokerani ku Makedoniya.” (Mac. 16:9) Atafika anakumana ndi mzimayi wina dzina lake Lidiya amene ‘anali kumvetsera ndipo Yehova anatsegula kwambiri mtima wake’ kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 16:14) Pasanapite nthawi yaitali, anabatizidwa limodzi ndi anthu a m’banja lake. Koma Mdyerekezi anabweretsa mavuto ambiri. Anthu amumzindawo anagwira Paulo ndi Sila n’kupita nawo kwa akuluakulu a boma ndipo anawanamizira kuti akuyambitsa chisokonezo. Kenako anawamenya, kuwaika m’ndende ndipo patapita nthawi anawalamula kuti achoke mumzindawo. (Mac. 16:16-40) Koma iwo sanabwerere m’mbuyo. Kodi abale ndi alongo amumpingo umene unali utangokhazikitsidwa kumenewo anatani? N’zosangalatsa kuti nawonso anapirira. N’zosakayikitsa kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi chitsanzo cha Paulo komanso Sila. w19.08 2 ¶1-2
Loweruka, September 11
Mudzazidwe ndi zipatso zolungama.—Afil. 1:11.
N’zosakayikitsa kuti zina mwa ‘zipatso zolungamazi’ zinali kukonda Yehova komanso anthu ake. Zipatsozi zimaphatikizanso kuuza anthu ena chifukwa chake timakhulupirira Yesu komanso zinthu zabwino zimene timayembekezera. Timabala “zipatso zolungama” tikamagwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:18-20) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tonsefe tikhoza kuwala monga zounikira. Nthawi zina, zinthu zimene zingaoneke kuti zingatilepheretse kulalikira uthenga wabwino zikhoza kutipatsa mwayi woti tilalikire anthu ena. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anali pa ukaidi wosachoka panyumba ku Roma pa nthawi imene analembera kalata Akhristu a ku Filipi. Komabe iye ankakwanitsa kulalikira kwa anthu omulondera komanso amene ankabwera kudzamuona. Paulo ankalalikirabe mwakhama ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto amenewa ndipo zimenezi zinalimbikitsa abale kuti azilankhula “mawu a Mulungu mopanda mantha.”—Afil. 1:12-14; 4:22. w19.08 12 ¶15-16
Lamlungu, September 12
Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.—1 Pet. 5:6.
Chifukwa chachikulu chotichititsa kukhala odzichepetsa n’chakuti Yehova amasangalala ndi khalidweli. Mtumwi Petulo anasonyeza mfundo imeneyi momveka bwino pamene analemba mawu amulemba la lero. Pofotokoza zimene Petulo ananena, buku lakuti ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga,’ mutu 3, ndime 23, limanena kuti: “Kudzikuza kuli ngati poizoni, ndipo kumawononga zinthu kwambiri. Munthu amene ali ndi luso lotha kuchita bwino zinthu zosiyanasiyana angakhale wachabechabe m’maso mwa Mulungu ngati wayamba kudzikuza. Koma munthu wodzichepetsa, ngakhale atakhala wooneka ngati wonyozeka, amakhala wamtengo wapatali kwa Yehova. . . . [Yehovayo] adzasangalala kukupatsani inunso mphoto chifukwa cha kudzichepetsa kwanu.” Kunena zoona, palibe chinthu china chabwino kuposa kusangalatsa mtima wa Yehova. (Miy. 23:15) Kuwonjezera pa kusangalatsa Yehova, timadalitsidwa kwambiri tikamayesetsa kukhala odzichepetsa. Tikakhala odzichepetsa anthu ambiri amafuna kukhala anzathu. Inunso muyenera kuti mumasangalala kucheza ndi anthu odzichepetsa.—Mat. 7:12. w19.09 4 ¶8-9
Lolemba, September 13
Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.—Miy. 16:5.
Akulu ayenera kuyesetsa kuthandiza abale ndi alongo. Komanso sayenera kudziona kuti ndi apamwamba chifukwa cha udindo wawo. M’malomwake ayenera kuchita zinthu mwachikondi ndi anthu mumpingo. (1 Ates. 2:7, 8) Chikondi komanso kudzichepetsa ziyenera kuwathandiza kuti azilankhula ndi abale ndi alongo mokoma mtima. M’bale wina dzina lake Andrew, yemwe wakhala mkulu kwa zaka zambiri, ananena kuti: “Ndimaona kuti akulu akamachita zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi amathandiza kwambiri abale ndi alongo. Makhalidwe amenewa amathandiza kuti abale ndi alongo azigwirizana ndi akulu.” M’bale wina dzina lake Tony, amene wakhalanso mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Ndimayesetsa kutsatira malangizo a pa Afilipi 2:3 oti tiziona ena kukhala otiposa. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizipewa kupondereza anthu ena.” Akulu ayenera kukhala odzichepetsa ngati Yehova. Ngakhale kuti Yehova ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse, iye “amatsika m’munsi” kuti adzutse “munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.” (Sal. 18:35; 113:6, 7) Ndipo Yehova amanyansidwa ndi anthu onyada komanso odzikweza. w19.09 16-17 ¶11-12
Lachiwiri, September 14
Senzani goli langa.—Mat. 11:29.
Kuti tipitirize kutsitsimulidwa posenza goli la Yesu, tiyenera kuona zinthu moyenera. Ntchito imene timagwira ndi ya Yehova choncho tiyenera kuigwira m’njira imene iye akufuna. Paja ife ndife antchito ndipo Yehova ndi Ambuye wathu. (Luka 17:10) Tikamagwira ntchitoyi m’njira yathuyathu tidzapeza kuti tikuvutika kusenza golilo. Koma tikamatsatira malangizo a Yehova tikhoza kuchita zinthu zikuluzikulu komanso kuthana ndi vuto lililonse. Tisaiwale kuti palibe amene angalepheretse Yehova kukwaniritsa zimene akufuna. (Aroma 8:31; 1 Yoh. 4:4) Cholinga chathu ndi kulemekeza Atate wathu wachikondi, Yehova. Yesu ali padzikoli, anthu amene anali ndi cholinga chadyera kapena ankangofuna kupeza zinazake sanapitirize kukhala osangalala ndipo anasiya kusenza goli lake. (Yoh. 6:25-27, 51, 60, 66; Afil. 3:18, 19) Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene sanali odzikonda koma ankakonda Mulungu ndi anzawo ankasenza golili kwa moyo wawo wonse ndipo ankayembekezera kukatumikira ndi Khristu kumwamba. Nafenso tikamachita zinthu ndi cholinga chabwino tikhoza kusenza goli la Yesu mosangalala. w19.09 20 ¶1; 24-25 ¶19-20
Lachitatu, September 15
Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.—Yoh. 8:32.
Muli pa ufulu chifukwa choti mwamasulidwa ku ukapolo wotsatira zikhulupiriro zabodza. N’zosangalatsa kwambiri kukhala pa ufulu umenewu. Koma pali ufulu waukulu kwambiri umene tikuyembekezera. Posachedwapa, Yesu adzachotsa zipembedzo zonyenga komanso maboma achinyengo. Mulungu adzapulumutsa “khamu lalikulu” la anthu amene amamutumikira kuti apeze madalitso osaneneka m’dziko latsopano. (Chiv. 7:9, 14) Anthu ambirimbiri adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi woti amasulidwe ku uchimo umene tinatengera kwa Adamu. (Mac. 24:15) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu ndi mafumu anzake adzathandiza anthu onse kuti akhale angwiro. Nthawi imeneyi idzakhala ngati Chaka cha Ufulu ku Isiraeli. Anthu onse padzikoli amene amatumikira Yehova mokhulupirika adzamasulidwa ku uchimo n’kukhala angwiro. w19.12 12-13 ¶14-16
Lachinayi, September 16
Baranaba anamuthandiza.—Mac. 9:27.
M’nthawi ya atumwi, munthu wina wamtima wopatsa dzina lake Yosefe (anamutchanso Baranaba) analola Yehova kuti amugwiritse ntchito. (Mac. 4:36, 37) Saulo atakhala Mkhristu abale ambiri ankamuopa chifukwa choti anali ndi mbiri yoti ankazunza Akhristu. Koma Baranaba anamuchitira chifundo ndipo anamuthandiza. (Mac. 9:21, 26-28) Pa nthawi ina, akulu a ku Yerusalemu ankafuna kulimbikitsa abale amene ankakhala kutali ku Antiokeya wa ku Siriya. Ndiye kodi anasankha kutumiza ndani? Iwo anasankha bwino kwambiri chifukwa anatumiza Baranaba. Baibulo limanena kuti Baranaba “anayamba kulimbikitsa onse kuti apitirize kukhala okhulupirika kwa Ambuye motsimikiza mtima.” (Mac. 11:22-24) Yehova angatithandizenso ifeyo kuti tikhale ngati Baranaba potonthoza Akhristu anzathu. Mwachitsanzo, angatigwiritse ntchito kutonthoza anthu amene aferedwa. Apo ayi, angatilimbikitse kuti tikaone kapena kuimbira foni munthu amene akudwala kapena akuvutika maganizo. Kodi inunso mudzalola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito ngati mmene anachitira ndi Baranaba?—1 Ates. 5:14. w19.10 22 ¶8
Lachisanu, September 17
Wophimba machimo akufunafuna chikondi, ndipo amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.—Miy. 17:9.
Nthawi zina tikamagwira ntchito kwambiri ndi anzathu timaona makhalidwe awo abwino komanso zimene amalakwitsa. Ndiye kodi tingatani kuti tizigwirizana nawobe? Tisamayembekezere kuti abale ndi alongo athu azichita zinthu zonse popanda kulakwitsa. Ndiye tikapeza anzathu apamtima, timafunika kuchita khama kuti tipitirizebe kugwirizana nawo. Anzathu akalakwitsa, tingafunike kuwapatsa malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu mwachikondi koma mosapita m’mbali. (Sal. 141:5) Ndipo akatikhumudwitsa tiyenera kuwakhululukira. Tikatero, tiyenera kupewa kukumbutsanso nkhaniyo. Masiku otsiriza ano, tiyenera kumaganizira kwambiri zinthu zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita osati zomwe amalakwitsa. Zimenezi zimathandiza kuti tizigwirizana kwambiri. Ndipo kugwirizana n’kofunika kwambiri chifukwa pa nthawi ya chisautso chachikulu tidzafunikira kukhala ndi anzathu apamtima. w19.11 6 ¶13, 16
Loweruka, September 18
Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mat. 28:19, 20.
Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti ‘akhale ophunzira komanso kuwaphunzitsa kuti asunge zinthu zonse zimene Yesu analamula.’ Tiyenera kuthandiza anthu kuti adziwe kufunika kokhala kumbali ya Yehova komanso Ufumu wake. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kulimbikitsa anthu kuti azitsatira mfundo zimene amaphunzira m’Baibulo, adzipereke kwa Yehova ndiponso abatizidwe. Zimenezi n’zimene zingawathandize kuti adzapulumuke pa tsiku la Yehova. (1 Pet. 3:21) Nthawi imene yatsala ndi yochepa kwambiri. Choncho tilibe nthawi yoti tiziphunzira ndi anthu amene sakusonyeza kuti akufuna kukhala ophunzira a Khristu. (1 Akor. 9:26) Ntchito yathu ndi yofunika kuigwira mwamsanga. Ndipo pali anthu ambiri amene akufunika kumva uthenga wa Ufumu nthawi isanathe. w19.10 11-12 ¶14-15
Lamlungu, September 19
Aziika zofukizazo pamoto umene uli pamaso pa Yehova.—Lev. 16:13.
Chaka chilichonse pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, Aisiraeli onse ankakumana n’cholinga choti apereke nsembe. Nsembe zimenezi zinkathandiza Aisiraeli kukumbukira kuti ndi ochimwa ndipo ankafunika kuyeretsedwa. Koma poyamba mkulu wa ansembe ankayenera kuthira zonunkhira zopatulika pamakala amoto ndipo m’chipinda chonse cha Malo Oyera Koposa munkamveka kafungo kabwino. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimenezi? Baibulo limasonyeza kuti mapemphero ovomerezeka a atumiki okhulupirika a Yehova ali ngati zofukiza zonunkhira. (Sal. 141:2; Chiv. 5:8) Mkulu wa ansembe ankapita mwaulemu kwambiri kukapereka zonunkhirazo pamaso pa Yehova. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kupereka mapemphero athu kwa Yehova mwaulemu kwambiri. Timalemekeza kwambiri Mlengi wathu komanso kuyamikira kuti amatipatsa mwayi woti tizigwirizana naye ngati mmene bambo amachitira ndi mwana wake. (Yak. 4:8) Ndipo iye amalola kuti tikhale anzake. (Sal. 25:14) Timayamikira mwayi wamtengo wapatali umenewu moti sitifuna kumukhumudwitsa ngakhale pang’ono. w19.11 20-21 ¶3-5
Lolemba, September 20
Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu. Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.—Sal. 104:24.
Kodi maganizo a anthu pa nkhani ya ntchito ndi otani kumene mumakhala? M’mayiko ena anthu akulimbikira kwambiri ntchito ndipo akumagwira nthawi yaitali kuposa m’mbuyomu. Anthu oterewa sakhala ndi nthawi yopuma, yocheza ndi mabanja awo kapena yophunzira za Mulungu. (Mlal. 2:23) Koma anthu ena safuna kugwira ntchito ngakhale pang’ono ndipo amapeza zifukwa zodzikhululukira. (Miy. 26:13, 14) Koma maganizo a Yehova ndi Yesu pa nkhani ya ntchito ndi osiyana kwambiri ndi a anthu ambiri m’dzikoli. N’zosachita kufunsa kuti Yehova amagwira ntchito. Paja Yesu ananena kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.” (Yoh. 5:17) Taganizirani ntchito yaikulu imene Mulungu anagwira polenga kumwamba komanso angelo osawerengeka. Yehova anagwiranso ntchito polenga zinthu zambiri zokongola zomwe zili padziko lapansili. w19.12 2 ¶1-2
Lachiwiri, September 21
Ndapeza Davide . . . munthu wapamtima panga.—Mac. 13:22.
Kodi zinatani kuti Davide ayambe kugwirizana kwambiri ndi Yehova? Davide anaphunzira za Yehova poona chilengedwe. Davide ali wamng’ono ankakhala nthawi yaitali akuweta nkhosa za bambo ake. N’kutheka kuti pa nthawi imeneyi m’pamene anayamba kuganizira kwambiri zinthu zimene Yehova analenga. Mwachitsanzo, iye akayang’ana kumwamba sankangoona nyenyezi basi. Ayenera kuti ankazindikiranso makhalidwe a amene analenga nyenyezizo. (Sal. 19:1, 2) Iye akaganizira mmene Yehova analengera anthu ankaona kuti Yehovayo ndi wanzeru kwambiri. (Sal. 139:14) Iye akaganizira zinthu zonse zimene Yehova wachita ankazindikira kuti ndi wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi Yehovayo. (Sal. 139:6) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tsiku lililonse tiziganizira zimene tingaphunzire zokhudza Yehova pa zinthu monga zomera, nyama komanso anthu. Tikatero, tsiku ndi tsiku tiziphunzira zinthu zambiri zokhudza Atate wathu. (Aroma 1:20) Zimenezi zidzathandiza kuti chikondi chathu kwa iye chiziwonjezereka tsiku lililonse. w19.12 19-20 ¶15-17
Lachitatu, September 22
Mwa chikhulupiriro, Mose atakula anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao.—Aheb. 11:24.
Mose anasankha kutumikira Mulungu. Mose ali ndi zaka pafupifupi 40, anasankha kugwirizana ndi Aheberi, omwe anali anthu a Mulungu, m’malo motchedwa “mwana wa mwana wamkazi wa Farao.” Iye analolera kuti asakhale ndi udindo wapamwamba koma agwirizane ndi Aheberi, omwe anali akapolo ku Iguputo. Zimenezi zikanachititsa kuti Farao, yemwe anali wolamulira wamphamvu komanso anthu ankamuona kuti anali mulungu, amukwiyire kwambiri. Apatu Mose anasonyeza chikhulupiriro cholimba. Iye ankadalira Yehova ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova moyo wake wonse. (Miy. 3:5) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mose? Tonsefe tiyeneranso kusankha zochita pa nkhani yotumikira Mulungu komanso kugwirizana ndi anthu ake. Mwina tingafunike kudzimana zinthu zina kuti tizitumikira Mulungu ndipo anthu amene sadziwa Yehova akhoza kutitsutsa. Koma tikamadalira Atate wathu wakumwamba, iye sangatisiye. w19.12 17 ¶5-6
Lachinayi, September 23
Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi, ndipo anauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake.—Gen. 2:7.
N’zoona kuti tinapangidwa kuchokera ku fumbi, koma anthufe ndi amtengo wapatali. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ndife amtengo wapatali kwa Yehova? Iye analenga anthu m’njira yoti azitha kutengera makhalidwe ake. (Gen. 1:27) Apatu anatilemekeza kuposa zinthu zina zonse zapadzikoli ndipo anatipatsa udindo woyang’anira dziko lapansi komanso nyama. (Sal. 8:4-8) Mulungu sanasiye kulemekeza anthu ngakhale Adamu atachimwa. Iye amatiwerengera kwambiri moti anapereka Mwana wake wokondedwa kuti akhale dipo lotiwombola. (1 Yoh. 4:9, 10) Chifukwa cha dipoli, Yehova adzatha kuukitsa anthu “olungama ndi osalungama” amene anafa chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu. (Mac. 24:15) Mawu ake amasonyeza kuti iye amationa kuti ndife amtengo wapatali mosaganizira za thanzi lathu, chuma chathu kapena msinkhu wathu.—Mac. 10:34, 35. w20.01 15 ¶5-6
Lachisanu, September 24
[Musamalowerere] nkhani za eni.—1 Ates. 4:11.
Nkhani yodzozedwa imachokera kwa Mulungu osati m’banja. (1 Ates. 2:12) Choncho tizipewa kufunsa mafunso amene akhoza kukhumudwitsa anthu ena. Mwachitsanzo, si bwino kufunsa mkazi wa m’bale wodzozedwa kuti, ‘Kodi mumamva bwanji mukaganiza kuti mudzakhala ndi moyo wosatha padzikoli mwamuna wanu kulibe?’ Paja tonse sitikayikira kuti m’dziko latsopano Yehova ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’ (Sal. 145:16) Timadzitetezanso tikamapewa kuona kuti odzozedwa ndi ofunika kwambiri kuposa anthu ena. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limasonyeza kuti mwina odzozedwa ena angasiye kukhala okhulupirika. (Mat. 25:10-12; 2 Pet. 2:20, 21) Choncho tikamapewa ‘kutamanda anthu ena’ zimatithandiza kuti tisamangowatsatira ngakhale atakhala kuti ndi odzozedwa, odziwika kwambiri kapena amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali. (Yuda 16) Ndiye ngati atakhala osakhulupirika kapena kuchoka mumpingo, sitingasiye kukhulupirira Yehova kapena kumutumikira. w20.01 29 ¶9-10
Loweruka, September 25
Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.
Popeza ndife ‘ana okondedwa’ a Yehova, timayesetsa kumutsanzira. Timatsanzira makhalidwe ake tikamachitira ena zinthu mwachikondi, mwachifundo komanso kuwakhululukira. Anthu amene sadziwa Mulungu akamaona makhalidwe athu abwino, zingawachititse kufuna kuti amudziwe bwino. (1 Pet. 2:12) Makolo achikhristu ayenera kutsanzira Yehova pochita zinthu ndi ana awo. Akamachita zimenezi, anawo angakhale ndi mtima wofuna kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Atate wathu wachikondi. Timanyadira kwambiri Atate wathu wakumwamba Yehova ndipo timafuna kuti ena amudziwe. Timamva ngati mmene Mfumu Davide ankamvera. Iye analemba kuti: “Ndidzadzitamandira mwa Yehova.” (Sal. 34:2) Koma ngati ndife amanyazi, kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima? Timalimba mtima tikamakumbukira kuti Yehova amasangalala tikamalalikira komanso kuti anthu amene angatimvetsere adzapeza madalitso. Yehova adzatithandiza kukhala olimba mtima. Iye anathandiza Akhristu oyambirira kulimba mtima ndipo adzatithandizanso ifeyo.—1 Ates. 2:2. w20.02 11 ¶12-13
Lamlungu, September 26
Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.—Mat. 28:19.
Anthu ambiri amene amaphunzira Baibulo amafika pobatizidwa. Koma zikuoneka kuti anthu ena amene timaphunzira nawo amachita mantha kuti akhale ophunzira a Yesu. Iwo amasangalala kuphunzira koma sasintha kuti afike pobatizidwa. Ngati mukuphunzira ndi munthu, n’zosachita kufunsa kuti mumafuna kumuthandiza kuti azitsatira zimene akuphunzirazo kuti akhale wophunzira wa Khristu. Yehova amafuna kuti anthu azimutumikira chifukwa chomukonda. Choncho cholinga chathu n’chothandiza anthu kuzindikira kuti Yehova amawakonda kwambiri komanso amawafunira zabwino. Timafuna kuwathandiza kuzindikira kuti Yehova ndi “tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu.” (Sal. 68:5) Anthu akazindikira kuti Yehova amawakonda akhoza kumva bwino ndipo angayambenso kumukonda kwambiri. Choncho mukamaphunzira ndi anthu muziwathandiza kuzindikira kuti Mulungu amafuna kuti iwo adzapeze moyo wosatha ndipo angawathandize kuti zimenezi zitheke. w20.01 3 ¶7-8
Lolemba, September 27
Chikondi chako m’bale chandisangalatsa ndi kundilimbikitsa kwambiri.—Filim. 7.
Mtumwi Paulo anali wodzichepetsa choncho ankapempha komanso kulola kuti anzake azimulimbikitsa. N’zoonekeratu kuti sankadera nkhawa zoti ena azimuona ngati wofooka chifukwa cholola kuti anthu ena amulimbikitse pa nthawi ya mavuto. (Akol. 4:7-11) Tikavomereza modzichepetsa kuti tikufunika kulimbikitsidwa, abale ndi alongo athu adzatithandiza mosangalala. Paulo ankadziwa kuti Malemba angamulimbikitse. (Aroma 15:4) Ankadziwanso kuti angamupatse nzeru zomuthandiza akakumana ndi mavuto. (2 Tim. 3:15, 16) Atamangidwa kachiwiri ku Roma, Paulo ankaona kuti imfa yake yayandikira. Ndiye anapempha Timoteyo kuti abwere msanga komanso amubweretsere “mipukutu.” (2 Tim. 4:6, 7, 9, 13) Paulo anachita zimenezi chifukwa mipukutuyo iyenera kuti inali mbali za Malemba Achiheberi zimene akanagwiritsa ntchito pophunzira payekha. Tikamatsanzira Paulo pophunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, Yehova adzagwiritsa ntchito Malemba potitonthoza, ngakhale mavuto athu atakhala aakulu. w20.02 23-24 ¶14-15
Lachiwiri, September 28
Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.—Mat. 7:1.
Elifazi, Bilidadi ndi Zofari atapita kukaona Yobu, anakhala nthawi yaitali osalankhula kalikonse. Zimene analankhula pambuyo pake zimasonyeza kuti nthawi imene anakhala cheteyo sankaganizira mmene angathandizire Yobu. M’malomwake ankaganizira mmene angasonyezere kuti Yobu walakwitsa zinazake. Mfundo zina zimene ananena zinali zolondola koma zinthu zambiri zimene ananena zokhudza Yobu komanso Yehova zinali zopweteka komanso zabodza. Iwo ankasonyeza kuti Yobu anali munthu woipa. (Yobu 32:1-3) Kodi Yehova anatani? Iye anakwiya kwambiri ndi anthu atatuwo. Ananena kuti anthuwo ndi opusa ndipo ayenera kupempha Yobu kuti awapempherere. (Yobu 42:7-9) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Elifazi, Bilidadi ndi Zofari anachita? Choyamba, si bwino kuweruza abale athu. (Mat. 7:2-5) Ndi bwino kuwamvetsera mosamala tisanayambe kulankhula. Tikatero tikhoza kumvetsa bwino mavuto amene akukumana nawo. (1 Pet. 3:8) Chachiwiri, ngati tikulankhula tizitsimikizira kuti tikulankhula mokoma mtima ndipo mfundo zathu ndi zoona. (Aef. 4:25) Chachitatu, zimene timalankhula kwa anzathu zimakhudza Yehova. w20.03 22-23 ¶15-16
Lachitatu, September 29
Muzipemphera pa chochitika chilichonse.—Aef. 6:18.
Nthawi zambiri tikamaphunzitsa anthu za Yehova ifenso timayamba kumudziwa bwino. Mwachitsanzo, timaona umboni wakuti Yehova ndi wachifundo akamatitsogolera kuti tipeze anthu amtima wabwino. (Yoh. 6:44; Mac. 13:48) Timaonanso mphamvu za Mawu a Mulungu zikuthandiza anthu amene timaphunzira nawo kuti asiye makhalidwe oipa n’kuyamba kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Komanso timaona umboni wakuti Mulungu ndi woleza mtima akamapatsa anthu am’gawo lathu mipata yambiri yoti aphunzire za iye n’kudzapulumuka. (Aroma 10:13-15) Kaya tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kuonabe kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wamtengo wapatali. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi kupemphera kwa iye. Anthu amagwirizana kwambiri akamakambirana momasuka. Choncho muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu popemphera kwa iye pafupipafupi ndipo musamaope kumuuza zamumtima mwanu. w19.12 19 ¶11, 13-14
Lachinayi, September 30
Machimo anu akhululukidwa.—1 Yoh. 2:12.
Zimenezi zimatikhazika mtima pansi kwambiri. Komanso monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzathetsa mavuto onse amene tikukumana nawo chifukwa cha Satana ndi dziko lakeli. (Yes. 65:17; 1 Yoh. 3:8; Chiv. 21:3, 4) Mfundo imeneyi imatithandiza kukhala ndi chiyembekezo champhamvu. Ngakhale kuti ntchito imene Khristu watipatsa si yophweka, iye walonjeza kuti akhala nafe n’kumatithandiza mpaka mapeto a dzikoli. (Mat. 28:19, 20) Kuzindikira mfundo imeneyi kumatithandiza kuti tizikhala olimba mtima. Ndipo mtima wathu ukakhala m’malo, tikakhala ndi chiyembekezo komanso tikakhala olimba mtima timakhala ndi mtendere wamumtima. Koma kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtendere wamumtima ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu? Tiyenera kutsanzira Yesu. Choyamba, tiyenera kupemphera kwambiri. Chachiwiri, tiyenera kumvera Yehova n’kumalalikira mwakhama ngakhale zinthu zitavuta kwambiri. Ndipo chachitatu, tiyenera kulola kuti anzathu atithandize. Tikatero, mtendere wa Mulungu udzateteza maganizo ndi mitima yathu. (Afil. 4:6, 7) Ndipo mofanana ndi Yesu, tingathe kugonjetsa mayesero alionse.—Yoh. 16:33. w19.04 13 ¶16-17