Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es21
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2021
  • Timitu
  • Lachisanu, October 1
  • Loweruka, October 2
  • Lamlungu, October 3
  • Lolemba, October 4
  • Lachiwiri, October 5
  • Lachitatu, October 6
  • Lachinayi, October 7
  • Lachisanu, October 8
  • Loweruka, October 9
  • Lamlungu, October 10
  • Lolemba, October 11
  • Lachiwiri, October 12
  • Lachitatu, October 13
  • Lachinayi, October 14
  • Lachisanu, October 15
  • Loweruka, October 16
  • Lamlungu, October 17
  • Lolemba, October 18
  • Lachiwiri, October 19
  • Lachitatu, October 20
  • Lachinayi, October 21
  • Lachisanu, October 22
  • Loweruka, October 23
  • Lamlungu, October 24
  • Lolemba, October 25
  • Lachiwiri, October 26
  • Lachitatu, October 27
  • Lachinayi, October 28
  • Lachisanu, October 29
  • Loweruka, October 30
  • Lamlungu, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2021
es21

October

Lachisanu, October 1

Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.—2 Mbiri 16:9.

Tili ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Yehova amateteza anthu ake masiku ano. Mwachitsanzo, tikutha kulalikira komanso kuphunzitsa anthu choonadi padziko lonse. (Mat. 28:19, 20) Tikamachita zimenezi timathandiza anthu kudziwa ziwembu za Satana. Satana akanakhala ndi mphamvu zambiri akanatha kuletseratu ntchito yathu, koma sangathe. Ndiye tisamaope mizimu yoipa. Ngati ndife okhulupirika kwa Yehova, ziwanda sizingatiwonongeretu. Tonsefe tiyenera kukana zamizimu n’kumadalira Yehova. Tikatero, tidzadalitsidwa kwambiri ndipo sitidzapusitsidwa ndi mabodza a Satana. Komanso sitingasowe mtendere chifukwa choopa ziwanda. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tidzalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Paja Yakobo analemba kuti: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani. Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”​—Yak. 4:7, 8. w19.04 24 ¶15; 25 ¶18

Loweruka, October 2

Chipatso cha mimba ndicho mphoto.​—Sal. 127:3.

Ana anu ndi “cholowa chochokera kwa Yehova,” kapena kuti mphatso imene iye wakupatsani. Choncho ndi udindo wa makolo kuteteza anawo. Kodi mungateteze bwanji ana anu kuti asagwiriridwe? Choyamba, muyenera kudziwa zambiri zokhudza anthu ogwirira ana. Muyenera kudziwa za anthu amene amagwirira ana komanso zimene amachita pofuna kuwanyengerera. Nthawi zonse muyenera kukhala tcheru kuti muzindikire ngati ana anu angakhale pa ngozi. (Miy. 22:3; 24:3) Muzikumbukira kuti nthawi zambiri ana amagwiriridwa ndi munthu amene akumudziwa komanso kumukhulupirira. Chachiwiri, muzicheza ndi ana anu momasuka. (Deut. 6:6, 7) Kuti muchite zimenezi, muyenera kumvetsera bwino ana anu akamalankhula. (Yak. 1:19) Muyenera kukumbukira kuti ana amene agwiriridwa amaopa kuuza anthu ena. Mwina amaganiza kuti anthu sangawakhulupirire, apo ayi munthu amene wawagwirirayo akhoza kuwaopseza kuti asaulule. Ngati mukukayikira kuti mwina zinazake zachitika, muyenera kuwafunsa mafunso mokoma mtima ndipo muziwamvetsera moleza mtima akamafotokoza. Chachitatu, muziphunzitsa ana anu. Muziwaphunzitsa zimene anganene komanso kuchita ngati munthu wina akufuna kuwagwira mosayenera. w19.05 13 ¶19-22

Lamlungu, October 3

Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.—Miy. 16:5.

N’chifukwa chiyani Yehova amanyansidwa ndi anthu onyada? Chifukwa chimodzi n’chakuti anthu onyada komanso odzikonda amafanana ndi Satana. Tangoganizani, Satana ankafuna kuti Yesu, amene Mulungu anamugwiritsira ntchito polenga zinthu zonse, agwade n’kumulambira. (Mat. 4:8, 9; Akol. 1:15, 16) Anthu amene amadziona kuti ndi ofunika kwambiri amapereka umboni wakuti nzeru za m’dzikoli ndi zopusa kwa Mulungu. (1 Akor. 3:19) Koma Baibulo limatithandiza kuti tizidziona m’njira yoyenera. Limavomereza kuti aliyense ayenera kudzikonda moyenera. Paja Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mat. 19:19) Koma Baibulo siliphunzitsa kuti tiziganiza kuti ndife apamwamba kuposa anthu ena. M’malomwake, limanena kuti: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”​—Afil. 2:3; Aroma 12:3. w19.05 24 ¶13-14

Lolemba, October 4

Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma 12:2.

Kodi ndi zinthu ziti zimene munafunika kusintha mutaphunzira Mawu a Mulungu n’kusankha zoti muyambe kutumikira Yehova? Ambirife tinafunika kusintha makhalidwe ena oipa. (1 Akor. 6:9-11) Ndipo timayamikira kuti Yehova anatithandiza kusintha makhalidwewo. Komabe sitiyenera kukhutira ndi zimene tinasintha basi. N’zoona kuti tasiya kuchita machimo akuluakulu amene tinkachita tisanabatizidwe. Koma tiyenera kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingatichititse kuyambiranso khalidwe loipalo. Ndipo timafunika kuchita zinthu ziwiri. Choyamba, tiyenera kupewa ‘kutengera nzeru’ za dzikoli. Chachiwiri, tiyenera “kusandulika” mwa kusintha maganizo athu. Mawu akuti kusandulika amatanthauza zambiri osati kungosintha maonekedwe. Amatanthauza kusintha mbali zonse za moyo wathu. Tiyenera kusintha mtima wathu, zimene timalakalaka komanso mmene timaonera zinthu. w19.06 9 ¶4-6

Lachiwiri, October 5

Inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.​—Sal. 86:17.

Tikakhala ndi nkhawa, tikhoza kupeza mphamvu tikamapita kumisonkhano. Tikamasonkhana timapatsa Yehova mipata yoti ‘azitithandiza ndiponso kutilimbikitsa.’ Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera, Mawu ake komanso anthu ake kuti azitilimbikitsa kumisonkhano. Misonkhano imatipatsanso mwayi woti ‘tizilimbikitsana.’ (Aroma 1:11, 12) Mlongo wina dzina lake Sophia ananena kuti: “Yehova komanso abale ndi alongo athu ndi amene anandithandiza kuti ndipirire. Ndinkaona kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri. Ndipo ndazindikiranso kuti ndikamachita zambiri mumpingo komanso mu utumiki, ndimatha kupirira mavuto anga.” Tikakhala ndi nkhawa, tizikumbukira kuti Yehova analonjeza kuti adzatithandiza panopa kuti tipirire ndipo adzathetsa mavuto athu m’tsogolo. Tikakhumudwa kwambiri, Yehova akhoza kutipatsa mtima wofuna kusintha komanso mphamvu yoti tisinthire.​—Afil. 2:13. w19.06 19 ¶17-18

Lachitatu, October 6

Pitani, kauzeni abale anga, kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.​—Mat. 28:10.

Chinthu choyamba chimene Yesu anachita atangoukitsidwa chinali kukonza zoti akumane ndi ophunzira ake. Apa n’zodziwikiratu kuti ankafuna kuwapatsa malangizo ofunika kwambiri. Pamsonkhano umene Yesu anachita ndi ophunzira ake, iye ananena za ntchito yofunika imene ophunzirawo ankafunika kugwira, yomwe tikuigwiranso masiku ano. Iye anati: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mat. 28:19, 20) Yesu amafuna kuti otsatira ake onse azilalikira. Lamuloli sanalipereke kwa atumwi ake okhulupirika 11 okha. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi imene Yesu ankapereka lamuloli paphiri lina la ku Galileya panalinso anthu ena osati atumwi okha. Paja mngelo anawauza azimayi aja kuti: “Mukamuona [ku Galileya].” (Mat. 28:7) Zimenezi zikusonyeza kuti azimayi okhulupirika analiponso pamsonkhanowo. w20.01 2-3 ¶1-4

Lachinayi, October 7

Popeza simuli mbali ya dzikoli, koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.​—Yoh. 15:19.

Yesu anafotokoza chifukwa chake tiyenera kuyembekezera kuzunzidwa. Iye ananena kuti tidzadedwa chifukwa chakuti sitili mbali ya dziko. Choncho kuzunzidwa si umboni wakuti Yehova sakutidalitsa. Koma kumasonyeza kuti tikuchita zinthu zoyenera. Anthu alibe mphamvu zotilepheretseratu kulambira Yehova, yemwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Ambiri ayesapo kuchita zimenezi koma alephera. Chitsanzo ndi zimene zinachitika pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Pa nthawi imeneyi, maboma ambiri ankazunza koopsa anthu a Mulungu. Mwachitsanzo, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’mayiko olamulidwa ndi Germany komanso ku Australia, ku Canada ndi m’mayiko enanso. Koma kodi mukudziwa zomwe zinachitika? Pamene nkhondoyi inkayamba mu 1939, padziko lonse panali ofalitsa okwana 72,475. Koma malipoti akusonyeza kuti pamene nkhondoyi inkatha mu 1945, Yehova anali atadalitsa anthu ake moti chiwerengero chinawonjezeka kwambiri kufika 156,299. w19.07 9 ¶4-5

Lachisanu, October 8

Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.​—Yoh. 13:35.

Mwina panopa simukuphunzira Baibulo ndi munthu. Koma mukhoza kuthandiza anthu m’njira zina kuti akhale ophunzira. Mwachitsanzo, mungalandire anthu atsopano akabwera ku Nyumba ya Ufumu n’kumacheza nawo. Mukatero mudzawathandiza kuzindikira kuti ndife Akhristu enieni chifukwa choti timasonyeza chikondi. Ndemanga zimene mumapereka pamisonkhano, ngakhale zachidule, zingathandize anthu atsopano kuti adziwe mmene angayankhire mochokera mumtima komanso mwaulemu. Mukhozanso kupita ndi wofalitsa watsopano mu utumiki n’kumuthandiza kudziwa mmene angagwiritsire ntchito Malemba pokambirana ndi anthu. Mukamachita zimenezi, mumakhala kuti mukumuphunzitsa kuti azitsanzira Khristu. (Luka 10:25-28) Akhristu ambiri amatanganidwa chifukwa chokhala ndi maudindo ambiri. Komabe amapeza nthawi yophunzira Baibulo ndi anthu ndipo amasangalala kwambiri ndi ntchitoyi. w19.07 17 ¶11, 13

Loweruka, October 9

Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.—Afil. 3:13, 14.

Mtumwi Paulo sanalole kuti zinthu zabwino kapena zoipa zimene anachita m’mbuyo zimusokoneze. Paja iye ananena kuti “ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo,” kutanthauza kuti ankafuna kumaliza bwinobwino mpikisano. Kodi ndi zinthu ziti zimene Paulo sanalole kuti zizimusokoneza? Choyamba, panali zinthu zambiri zotamandika zimene anachita ali m’chipembedzo cha Chiyuda. Koma ankaona zinthu zonsezo ngati “mulu wa zinyalala.” (Afil. 3:3-8) Chachiwiri, iye sankalola kuti asokonezeke chifukwa chodziimba mlandu kuti anazunza kwambiri Akhristu. Chachitatu, iye sankaganiza kuti wachita kale zokwanira potumikira Yehova. Paulo anakwanitsa kuchita zambiri ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto monga kumangidwa, kumenyedwa, kugendedwa, kusweka kwa sitima komanso kusowa chakudya ndi zovala. (2 Akor. 11:23-27) Ngakhale kuti anali atachita kale zambiri komanso kukumana ndi mavuto, Paulo ankaona kuti afunika kuchitabe khama. Ndi mmene zililinso ndi ifeyo. w19.08 3 ¶5

Lamlungu, October 10

Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.​—Mat. 10:16.

Abale ndi alongo ambiri amakhala m’dziko limene mulibe ufulu wolalikira choncho amapeza njira zina zoti azilalikira. (Mat. 10:17-20) M’dziko lina, woyang’anira dera wina analimbikitsa wofalitsa aliyense kuti azilalikira anzake, achibale ake, anthu okhala nawo pafupi, anzake akusukulu komanso anzake akuntchito. Pasanathe zaka ziwiri, chiwerengero cha mipingo m’deralo chinawonjezereka kwambiri. Mwina m’dziko limene tikukhala muli ufulu wolalikira, koma tikhoza kutsatirabe chitsanzo cha abale ndi alongowa. Tingachite zimenezi poyesetsa nthawi zonse kupeza mpata wolalikira. Komanso tisamakayikire kuti Yehova adzatipatsa mphamvu yochitira zimenezi ngakhale tikukumana ndi mavuto. (Afil. 2:13) M’masiku otsirizawa, tiyeni tizitsimikizira kuti zinthu zofunika ndi ziti, tizikhala opanda cholakwa, tizipewa kukhumudwitsa ena komanso tizibala zipatso zolungama. Tikatero chikondi chathu chidzapitiriza kukula komanso tizilemekeza Yehova yemwe ndi Atate wathu wachikondi. w19.08 13 ¶17-18

Lolemba, October 11

Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi, koma akalonga akuyenda pansi ngati antchito.​—Mlal. 10:7.

Ambirife sitisangalala ndi anthu amene nthawi zonse amakakamira maganizo awo ndipo safuna kumva za ena. Koma timasangalala kuchita zinthu ndi abale ndi alongo ‘omvera ena chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu ndiponso amaganizo odzichepetsa.’ (1 Pet. 3:8) Popeza timasangalala ndi anthu odzichepetsa, iwonso angasangalale nafe ngati tili odzichepetsa. Kudzichepetsa kumathandizanso kuti zinthu zisamatisowetse mtendere. Kunena zoona, anthufe timakumana ndi zinthu zina zimene zimaoneka kuti si zachilungamo. Nthawi zina anthu aluso kwambiri sayamikiridwa pomwe amene ali ndi luso lochepa ndi amene amalemekezedwa. Koma Solomo ananena kuti ndi nzeru kungovomereza mmene zinthu zilili m’malo molimbana nazo. (Mlal. 6:9) Tikakhala odzichepetsa, sitingavutike kuvomereza mmene zinthu zilili m’malo mokakamira kuti zisinthe. w19.09 4-5 ¶9-10

Lachiwiri, October 12

Abambo, . . . muwalere [ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.​—Aef. 6:4.

Anthu amene apatsidwa udindo woyang’anira ena, monga abambo, akhoza kuthandiza kwambiri anthu. Yehova anapatsa abambo udindo woyang’anira banja ndipo amafuna kuti aziphunzitsa komanso kulangiza ana awo. (1 Akor. 11:3) Koma udindo wa abambo uli ndi malire. Tikutero chifukwa chakuti Yehova ndi amene anayambitsa banja ndipo akhoza kuimba bambo mlandu pa zimene amachita ndi anthu a m’banja lake. (Aef. 3:14, 15) Abambo amasonyeza kuti amagonjera Yehova potsogolera banja lawo m’njira imene imasangalatsa Mulungu. Simuyenera kugwiritsa ntchito molakwika udindo umene Yehova wakupatsani. Muyeneranso kuvomereza zimene mwalakwitsa n’kulandira malangizo ochokera m’Malemba amene mungapatsidwe. Mukamachita zimenezi anthu a m’banja lanu adzayamikira kudzichepetsa kwanu ndipo azikulemekezani. Popemphera ndi banja, muyenera kufotokoza zinthu kuchokera pansi pa mtima kuti anthu a m’banja lanu aziona kuti mumadalira kwambiri Yehova. Koma chofunika kwambiri n’chakuti muziika kutumikira Yehova pamalo oyamba. (Deut. 6:6-9) Chitsanzo chanu chabwino n’chimene chingathandize kwambiri anthu a m’banja lanu. w19.09 15 ¶8; 17 ¶14; 18 ¶16

Lachitatu, October 13

Mumulandire [Maliko] nthawi iliyonse akadzafika kwa inu.​—Akol. 4:10.

Maliko ankakonda kutumikira anthu ena. Iye ankatumikira limodzi ndi Paulo komanso Petulo. N’kutheka kuti ankawathandiza pa zinthu zina zofunika pa moyo kuti iwo asavutike kukwaniritsa utumiki wawo. (Mac. 13:2-5; 1 Pet. 5:13) Paulo ananena kuti Maliko anali mmodzi mwa ‘anzake pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:11) Maliko anali mmodzi mwa anthu amene ankagwirizana kwambiri ndi Paulo. Mwachitsanzo, pamene Paulo anamangidwa komaliza ku Roma cha m’ma 65 C.E., analemba kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo. M’kalatayo, Paulo anapempha Timoteyo kuti abwere ku Roma limodzi ndi Maliko. (2 Tim. 4:11) N’zosakayikitsa kuti Paulo ankayamikira zimene Maliko anachita pomuthandiza ndipo ankafuna kuti akhalenso naye pa nthawi yovutayi. N’kutheka kuti Maliko ankathandiza Paulo pomupatsa chakudya kapena zipangizo zogwiritsa ntchito polemba. Zimene anthu ena ankamuchitira Paulo zinamuthandiza kuti apirire mpaka pamene anaphedwa. w20.01 11 ¶12-13

Lachinayi, October 14

Bwerani kwa ine.​—Mat. 11:28.

Akhristufe tinasankha moyo wodzimana zinthu zina komanso wogwira ntchito mwakhama. Yesu anatichenjezanso kuti tidzazunzidwa. Koma tiyenera kuyembekezera kuti Yehova adzatipatsa mphamvu kuti tipirire vuto lililonse. Ndipo tikamapirira kwambiri m’pamene timakhalanso olimba kwambiri. (Yak. 1:2-4) Tisamakayikire kuti Yehova azitipatsa zimene tikufunikira, Yesu azititsogolera ngati m’busa wabwino komanso abale ndi alongo athu azitilimbikitsa. (Mat. 6:31-33; Yoh. 10:14; 1 Ates. 5:11) Mayi amene ankadwala matenda otaya magazi anatsitsimulidwa pa tsiku limene Yesu anamuchiritsa. (Luka 8:43-48) Koma kuti apitirize kutsitsimulidwa mpaka kalekale, anafunika kukhala wophunzira wokhulupirika wa Khristu. Kodi inuyo mukuganiza kuti mayiyu anatani? Ngati anasankha kusenza goli la Yesu, ndiye kuti anali ndi mwayi wokatumikira ndi Yesuyo kumwamba. Chilichonse chimene analolera kudzimana kuti azitsatira Khristu n’chaching’ono kwambiri poyerekezera ndi madalitso amenewa. Kaya tikuyembekezera moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, tiyenera kuyamikira kuti tinavomera pamene Yesu anatiuza kuti: “Bwerani kwa ine.” w19.09 25 ¶21-22

Lachisanu, October 15

Nzeru zimamanga banja la munthu, ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.​—Miy. 24:3.

Davide ndi anzake ankafuna thandizo ndipo anzakewo anakapempha chakudya kwa munthu wina wolemera dzina lake Nabala. Iwo sanaope kukapempha chifukwa choti anali atathandiza kuteteza ziweto zake m’chipululu. Koma Nabala anali wodzikonda ndipo anakana kuwapatsa chilichonse. Zitatero, Davide anakwiya kwambiri ndipo ankafuna kupha Nabala komanso mwamuna aliyense wa m’nyumba yake. (1 Sam. 25:3-13, 22) Koma mkazi wa Nabala, dzina lake Abigayeli, yemwe anali wokongola kwambiri analinso wanzeru. Iye analimba mtima n’kukagwada pamaso pa Davide ndipo anamuchonderera kuti asabwezere zoipazo n’kupalamula mlandu wa magazi. Iye anauza Davide mwaulemu kuti angosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Kudzichepetsa komanso nzeru za Abigayeli zinathandiza kwambiri Davide. Iye anafika poona kuti Yehova ndi amene anamutuma. (1 Sam. 25:23-28, 32-34) Abigayeli anali ndi makhalidwe amene anathandiza kuti agwiritsidwe ntchito ndi Yehova. Masiku anonso, alongo amene amachita zinthu mwanzeru akhoza kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova kuti alimbikitse anthu a m’banja lawo komanso amumpingo.​—Tito 2:3-5. w19.10 23 ¶10

Loweruka, October 16

Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.—Chiv. 18:4.

Akhristu onse oona ayenera kupeweratu chilichonse chogwirizana ndi Babulo Wamkulu. Zingachitike kuti munthu asanayambe kuphunzira Baibulo anali m’chipembedzo chonyenga. Pa nthawiyo, mwina ankachita nawo zinthu zina kapena kupereka ndalama zothandiza chipembedzo chimenecho. Choncho asanavomerezedwe kuti akhale wofalitsa wosabatizidwa, ayenera kusiya chilichonse chokhudzana ndi zipembedzo zonyenga. Ayenera kulemba kalata kapena kudziwitsa chipembedzo chake chakale m’njira inayake kuti wachokamo. Ayeneranso kuchita zimenezi ndi gulu lililonse limene limagwirizana ndi Babulo Wamkulu. Mkhristu aliyense ayenera kuonetsetsa kuti ntchito yake sikukhudzana ndi Babulo Wamkulu. (2 Akor. 6:14-17) N’chifukwa chiyani tiyenera kupeweratu chonchi? Chifukwa chakuti sitifuna kuthandiza nawo pa ntchito kapena machimo a zipembedzo zomwe ndi zodetsedwa pamaso pa Yehova.​—Yes. 52:11. w19.10 12 ¶16-17

Lamlungu, October 17

Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo . . . Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu, kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.—Sal. 103:8, 9.

Yeremiya analemba buku la m’Baibulo la Yeremiya komanso ayenera kuti analembanso mabuku a 1 Mafumu ndi 2 Mafumu. Polemba mabukuwa, ayenera kuti anazindikira kuti Yehova amasonyeza chifundo kwa anthu ochimwafe. Mwachitsanzo, anadziwa kuti Mfumu Ahabu atalapa, Yehova anasankha kuti asawononge anthu a m’banja lake onse pa nthawi imene iye anali moyo. (1 Maf. 21:27-29) Yeremiya anadziwanso kuti Manase anachita zinthu zoipa kwambiri kuposa Ahabu. Koma Yehova anamukhululukira chifukwa choti analapa. (2 Maf. 21:16, 17; 2 Mbiri 33:10-13) Nkhani zimenezi ziyenera kuti zinathandiza Yeremiya kuti azitsanzira Yehova pokhala woleza mtima komanso wachifundo Tiyeni tione zimene Yeremiya anachita Baruki atayamba kusokonezeka ndi zinthu zina. Iye sanafulumire kusiya kugwirizana ndi mnzakeyo. M’malomwake, anamuthandiza pomuuza uthenga wochokera kwa Mulungu womwe unali wachikondi koma wosapita m’mbali.​—Yer. 45:1-5. w19.11 6 ¶14-15

Lolemba, October 18

Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.​—Aheb. 6:10.

M’buku la Levitiko timaphunzira kuti Aisiraeli ankatha kupereka nsembe zachiyanjano “posonyeza kuyamikira.” (Lev. 7:11-13, 16-18) Iwo ankapereka nsembezi mwa kufuna kwawo osati chifukwa chotsatira lamulo linalake. Nafenso timatumikira Yehova mwa kufuna kwathu pofuna kusonyeza kuti timamukonda. Timapatsa Yehova zinthu zathu zabwino kwambiri chifukwa chomukonda ndi mtima wathu wonse. Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona atumiki ake mamiliyoni akumutumikira chifukwa choti amamukonda komanso amakonda njira zake. Timalimbikitsidwa tikakumbukira kuti Yehova amaona zimene timachita komanso chifukwa chimene timachitira zinthuzo ndipo amayamikira. Mwachitsanzo, ngati ndinu achikulire ndipo simungakwanitse kuchita zonse zimene mumafuna, dziwani kuti Yehova amakumvetsani. Mwina mumaona kuti mumachita zochepa, koma Yehova amadziwa kuti mumachita zimene mungathe chifukwa chomukonda kwambiri. Iye amasangalala kulandira zimene mungakwanitse kumupatsa. w19.11 22 ¶9; 23 ¶11-12

Lachiwiri, October 19

Bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.​—Maliko 6:31.

Tizikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito. Mfumu Solomo analemba kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake.” Iye anatchula za nthawi yobzala, yomanga, yolira, yoseka, yovina komanso ya zinthu zina. (Mlal. 3:1-8) Apa n’zoonekeratu kuti kugwira ntchito komanso kupuma ndi zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Yesu anali ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito komanso kupuma. Pa nthawi ina, atumwi anabwera kuchokera kokalalikira. Iwo anatanganidwa kwambiri moti “analibe nthawi yopuma, ngakhale yoti adye chakudya.” Kenako Yesu anawauza mawu a mulemba lalerowa. (Maliko 6:30-34) Ngakhale kuti nthawi zina Yesu ndi ophunzira ake sankapeza nthawi yokwanira yoti apume, iye ankadziwa kuti onsewo ankafunika kupuma. Anthufe nthawi zina timafunika kupuma kapena kusintha zochita. Umboni wake ndi lamulo lokhudza Sabata limene Mulungu anapatsa Aisiraeli. N’zoona kuti sitiyendera Chilamulo cha Mose. Koma zimene Mulungu ananena pa nkhani ya Sabata zingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito ndi kupuma. w19.12 3 ¶6-7

Lachitatu, October 20

Musamade nkhawa.​—Mat. 6:31.

Yehova analonjeza kuti azisamalira atumiki ake okhulupirika ndipo amaona kuti ali ndi udindo wokwaniritsa lonjezoli. (Sal. 31:1-3) Yehova amadziwa kuti tikhoza kukhumudwa kwambiri ngati atapanda kusamalira ana ake. Iye analonjeza kuti adzatipatsa zofunika pa moyo komanso kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi ndipo palibe chimene chingamulepheretse kukwaniritsa lonjezoli. (Mat. 6:30-33; 24:45) Tikamakumbukira chifukwa chake Yehova amakwaniritsa malonjezo ake, sitidzakayikira kuti adzatithandiza tikakumana ndi mavuto azachuma. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Akhristu oyambirira. Atayamba kuzunzidwa ku Yerusalemu, ‘onse anabalalika kupatulapo atumwi okha.’ (Mac. 8:1) Apa n’zosachita kufunsa kuti anakumana ndi mavuto azachuma. Ambiri ayenera kuti anasiya nyumba ndi mabizinezi awo. Koma Yehova sanawasiye ndipo ankakhalabe osangalala. (Mac. 8:4; Aheb. 13:5, 6; Yak. 1:2, 3) Ngati Yehova anathandiza Akhristu okhulupirikawa, ndiye kuti ifenso angatithandize.​—Sal. 37:18, 19. w20.01 17-18 ¶14-15

Lachinayi, October 21

Yehova . . . amaona wodzichepetsa.​—Sal. 138:6.

Davide atapha mkango ndi chimbalangondo zimene zinkafuna kugwira nkhosa za bambo ake, anazindikira kuti Yehova ndi amene anamuthandiza. Iye atagonjetsa Goliyati, anaonanso kuti Yehova ndi amene ankamutsogolera. (1 Sam. 17:37) Atapulumuka pamene Sauli ankafuna kumupha, Davide anaonanso kuti Yehova ndi amene wamupulumutsa. (Sal. 18, timawu tapamwamba) Iye akanakhala wodzikuza bwenzi akudzitama pa zinthu zonsezi. Koma popeza Davide anali wodzichepetsa, anatha kuona kuti Yehova ndi amene ankamuthandiza. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tisamangopempha Yehova kuti atithandize. Koma tizizindikiranso mmene akutithandizira. Tikamazindikira zimene sitingakwanitse, zingakhale zosavuta kuti tione mmene Yehova akutithandizira. Nthawi iliyonse imene taona kuti Yehova watithandiza, ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambiri. w19.12 20 ¶18-19

Lachisanu, October 22

Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.​—Miyambo 3:12.

Pali zifukwa zambiri zosonyeza kuti ndife amtengo wapatali kwa Yehova. Iye anatikokera m’gulu lake ndipo anasangalala ataona zimene tinachita titamva uthenga wabwino. (Yoh. 6:44) Titayamba kuyandikira kwa iye, nayenso anatiyandikira. (Yak. 4:8) Yehova amayesetsanso kutiphunzitsa ndipo izi zimatitsimikizira kuti amatikonda kwambiri. Iye amadziwa mmene tilili panopa komanso mmene tingadzakhalire m’tsogolo. Ndipo amatipatsa malangizo chifukwa chotikonda. Wonsewutu ndi umboni wakuti ndife amtengo wapatali kwa Yehova. Mfumu Davide ankadziwa kuti Yehova amamukonda komanso kumuthandiza ngakhale kuti anthu ena ankamuona kuti ndi wachabechabe. Kudziwa zimenezi kunathandiza Davide kuti apirire mavuto ake. (2 Sam. 16:5-7) Ifenso tikakhumudwa kapena kukumana ndi mavuto enaake, Yehova akhoza kutithandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera n’kulimbana ndi vuto lililonse. (Sal. 18:27-29) Yehova akamatithandiza, palibe chilichonse chimene chingatilepheretse kumutumikira mosangalala.​—Aroma 8:31. w20.01 15 ¶7-8

Loweruka, October 23

[Muziwaphunzitsa] kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.—Mat. 28:20.

Mukamachititsa phunziro la Baibulo, muziyamba ndi pemphero. Ngati n’zotheka, musamadikire kuti muphunzire kaye ndi munthu maulendo ambiri musanayambe kutsegula ndiponso kutseka phunziro ndi pemphero. Tiyenera kuthandiza anthu kuzindikira kuti timafunika mzimu wa Yehova kuti tizimvetsa Mawu ake. Abale ndi alongo ena amafotokoza kufunika kwa pemphero powerenga lemba la Yakobo 1:5 lomwe limati: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu.” Kenako amafunsa munthu amene akuphunzira naye kuti, “Kodi tingapemphe bwanji Mulungu kuti atipatse nzeru?” Anthu ambiri angayankhe kuti tiyenera kupemphera kwa iye. Muziphunzitsa anthu kupemphera. Muziuza anthu kuti Yehova amafuna kumva mapemphero awo ochokera mumtima. Afotokozereni kuti tikamapemphera patokha tikhoza kuuza Yehova momasuka zimene zili mumtima mwathu zomwe sitingamasuke kuuza munthu wina. Paja Yehova amadziwa kale zonse zimene zili mumtima mwathu.​—Sal. 139:2-4. w20.01 2 ¶3; 5 ¶11-12

Lamlungu, October 24

Sizidalira munthu wofunayo kapena amene akuthamanga, koma Mulungu.​—Aroma 9:16.

Yehova amasankha nthawi imene akufuna kudzoza anthu. (Aroma 8:28-30) Yehova anayamba kusankha odzozedwa Yesu ataukitsidwa. Zikuoneka kuti nthawi ya atumwi, Akhristu onse anali odzozedwa. Pa zaka zambiri zotsatira, anthu ambiri amene ankati ndi Akhristu sanalidi otsatira enieni a Khristu. Ngakhale zinali choncho, pa nthawiyo Yehova ankadzozabe anthu ochepa amene anali Akhristu oona. Iwo anali ngati tirigu amene Yesu ananena kuti adzakulira limodzi ndi namsongole. (Mat. 13:24-30) M’masiku otsirizawa, Yehova wapitiriza kusankha anthu kuti akhale m’gulu la 144,000. Choncho ngati Mulungu atasankha kudzoza ena mapeto atatsala pang’ono kufika, sitiyenera kukayikira nzeru zake. (Aroma 9:11) Si bwino kuchita zinthu ngati antchito amene Yesu anawatchula m’fanizo lake lina. Iwo anadandaula ndi zimene mbuye wawo anachitira anthu amene anayamba kugwira ntchito pa ola lomaliza.​—Mat. 20:8-15. w20.01 30 ¶14

Lolemba, October 25

Atumiki anga adzafuula mokondwa.​—Yes. 65:14.

Yehova amafuna kuti ana ake azikhala osangalala. Pali zinthu zambiri zotichititsa kukhala osangalala panopa ngakhale tikukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, sitikayikira kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri. Timadziwanso mfundo zolondola za m’Mawu a Mulungu. (Yer. 15:16) Ndipo tili m’banja lapadera kwambiri la anthu amene amakonda Yehova ndi mfundo zake zapamwamba komanso amene amakondana. (Sal. 106:4, 5) Timakhalabe osangalala chifukwa sitikayikira kuti zinthu zidzakhala bwino kwambiri m’tsogolo. Tikudziwa kuti posachedwapa Yehova adzachotsa anthu onse oipa ndipo adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokonza dzikoli kuti likhale labwino kwambiri. Tilinso ndi chiyembekezo chakuti amene anamwalira adzaukitsidwa n’kumakhalanso limodzi ndi anzawo. (Yoh. 5:28, 29) Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa. Chofunika kwambiri n’chakuti posachedwapa, aliyense kumwamba komanso padziko lapansi adzakhala wodzipereka kwa Atate wathu wachikondi ndipo azidzamupatsa ulemu ndi ulemerero womuyenera. w20.02 13 ¶15-16

Lachiwiri, October 26

Ine ndakuchimwirani kwambiri.—Sal. 51:4.

Ngati mwachita tchimo lalikulu, musamabise zimene mwachitazo. Koma muzipemphera kwa Yehova n’kumuuza momasuka zimene mwalakwitsa. Izi zingakuthandizeni kuti musiye kudziimba mlandu komanso kuda nkhawa. Koma kuti mukonze ubwenzi wanu ndi Yehova, kungopemphera si kokwanira. Muyenera kuvomereza chilango chimene mwapatsidwa. Yehova atatumiza mneneri Natani kuti akauze Mfumu Davide za tchimo limene anachita ndi Batiseba, Davideyo sanapereke zifukwa zodzikhululukira kapena kupeputsa tchimolo. M’malomwake, nthawi yomweyo anavomereza kuti anachimwira mwamuna wa Batiseba koma kuposa zonse anachimwira Yehova. Davide anavomereza chilango chimene Yehova anamupatsa ndipo Yehova anamukhululukira. (2 Sam. 12:10-14) Ngati tachita tchimo lalikulu, tiyenera kulankhula ndi abale amene Yehova wawasankha kuti azitiyang’anira. (Yak. 5:14, 15) Tiyeneranso kupewa mtima wofuna kupereka zifukwa zodzikhululukira. Tikavomereza msanga chilango chimene tapatsidwa, tikhoza kupezanso mtendere mofulumira n’kumakhalanso osangalala. w20.02 24-25 ¶17-18

Lachitatu, October 27

Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—Zek. 8:23.

“Amuna 10” akuimira anthu amene akuyembekezera moyo wosatha padzikoli. Iwo amadziwa kuti Yehova akudalitsa odzozedwa amene “Myuda” akuimira ndipo ndi mwayi kutumikira nawo limodzi. N’zoona kuti masiku ano sitingadziwe mayina a odzozedwa onse amene ali padzikoli. Koma n’zotheka kuti amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli ‘apite nawo limodzi.’ Kodi tingapite nawo bwanji? Yankho tingalipeze mulemba laleroli. Onani kuti Baibulo likutchula za Myuda mmodzi. Koma mawu oti “anthu inu” komanso “inu” akunena za anthu ambiri. Zimenezi zikutanthauza kuti mawu oti Myuda sakunena za munthu mmodzi koma gulu lonse la odzozedwa. Anthu amene si odzozedwa amatumikira Yehova limodzi ndi odzozedwa. Koma saona kuti odzozedwawo ndi atsogoleri awo chifukwa Mtsogoleri wawo ndi Yesu.​—Mat. 23:10. w20.01 26 ¶1-2

Lachinayi, October 28

Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.​—Yoh. 13:35.

Yesu ananena kuti anthu angazindikire ophunzira ake ngati akukondana mmene iye ankawakondera. Zimene Yesu ananenazi zinali zoona mu nthawi ya atumwi ndipo ndi zoonanso masiku ano. N’chifukwa chake kukondana kwambiri n’kofunika ngakhale pamene zavuta. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndingaphunzire chiyani kwa abale ndi alongo omwe apitiriza kusonyezana chikondi ngakhale pali mavuto?’ Popeza si ife angwiro, zimativuta kuti tizikondana kwambiri. Komabe tiyenera kuyesetsa kutsanzira Khristu. Yesu anatiphunzitsa kufunika kokhazikitsa mtendere ndi anthu amene ali nafe chifukwa. (Mat. 5:23, 24) Iye ananena kuti tiyenera kukhala mwamtendere ndi anthu kuti tizisangalatsa Mulungu. Yehova amasangalala tikamayesetsa kuti tizikhala mwamtendere ndi abale athu. Iye sangasangalale ndi kulambira kwathu ngati timasungira ena zifukwa komanso kukana kukhazikitsa mtendere.​—1 Yoh. 4:20. w20.03 24 ¶1-4

Lachisanu, October 29

Mmenemu ndi mmene timadziwira mawu ouziridwa oona kapena abodza.​—1 Yoh. 4:6.

Satana ndi “tate wake wa bodza” ndipo wakhala akunamiza anthu kuyambira pamene anthu oyamba analengedwa. (Yoh. 8:44) Mabodza ena ndi okhudza imfa ndipo ena ndi okhudza zimene zimachitika pambuyo pa imfa. Zinthu zambiri zimene anthu amakhulupirira masiku ano zimachokera pa mabodza amenewa. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakhulupirira bodzali? Satana amadziwa mmene anthu ambiri amamvera pa nkhani ya imfa ndiye amapezerapo mwayi kuti awapusitse. Anthufe tinalengedwa kuti tisamafe choncho sitifuna kufa. (Mlal. 3:11) Tonse timaona kuti imfa ndi mdani wathu. (1 Akor. 15:26) Koma ngakhale kuti Satana wachita zonsezi, zoona zake pa nkhani ya imfa sizinabisike. Panopa anthu ambiri akudziwa komanso kuuza anzawo zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya imfa komanso zimene zidzachitikire akufa. (Mlal. 9:5, 10; Mac. 24:15) Kudziwa zoona pa nkhani ya akufa kumatilimbikitsa ndipo kumatithandiza kuti tisiye kuchita mantha kapena kukayikakayika. w19.04 14 ¶1; 15 ¶5-6

Loweruka, October 30

Musaleke kunyamulirana zolemetsa. Mukatero mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.​—Agal. 6:2.

Yehova Mulungu amakonda anthu amene amamulambira ndipo sadzasiya kuwakonda. Iye amakondanso chilungamo. (Sal. 33:5) Zimenezi zimatitsimikizira mfundo ziwiri izi: (1) Yehova zimamupweteka kwambiri akaona kuti atumiki ake akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo. (2) Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli kudzera mwa Mose chinapangidwa chifukwa cha chikondi. Chilamulocho chinkalimbikitsa kuti anthu onse, ngakhale anthu amene sankatha kudziteteza, azichitiridwa chilungamo. (Deut. 10:18) Chilamulochi chimasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake. Chilamulo cha Mose chinatha mu 33 C.E. pamene mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa. Kodi zimenezi zinatanthauza kuti panalibenso chilamulo cholimbikitsa chikondi ndi chilungamo chomwe Akhristu ankayenera kutsatira? Ayi. Akhristuwo anapatsidwa chilamulo chatsopano chomwe chinali “chilamulo cha Khristu.” Yesu sanalembe mndandanda wa malamulo, komabe anapatsa otsatira ake malangizo, malamulo komanso mfundo zoti azitsatira. “Chilamulo cha Khristu” chimaphatikizapo zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa. w19.05 2 ¶1-3

Lamlungu, October 31

Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”​—2 Akor. 1:3, 4.

Mwachibadwa, anthu amafuna kulimbikitsidwa komanso amakhala ndi luso lolimbikitsa anzawo. Mwachitsanzo, mwana akagwa n’kuvulala pamene akusewera, amathamangira mayi kapena bambo ake uku akulira. N’zoona kuti makolowo sangapoletse bala koma akhoza kutonthoza mwanayo. Akhoza kumufunsa zimene zachitika, kumupukuta misozi, kumutonthoza, mwinanso kumupaka mankhwala kapena kumumanga bandeji. Pasanathe nthawi yaitali, mwanayo amatonthola ndipo amakaseweranso. Pakapita nthawi, balalo limapola. Koma nthawi zina ana amapwetekedwa kwambiri. Mwachitsanzo, ena amagwiriridwa. Zimenezi zikhoza kuchitika kamodzi kapena mobwerezabwereza kwa zaka zambiri. Kaya zinachitika kangati, mfundo ndi yakuti kugwiriridwa kumasokoneza munthu kwa nthawi yaitali. Nthawi zina, wogwirira amagwidwa n’kulangidwa, pomwe ena salangidwa. Koma ngakhale wogwirirayo atalangidwa mwachilungamo, mwana amene wagwiriridwa akhoza kuvutika kwa zaka zambiri. w19.05 14 ¶1-2

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena