November
Lolemba, November 1
‘Muziona ena kukhala okuposani.’—Afil. 2:3.
Masiku ano, anthu ambiri omwe amaoneka kuti ndi anzeru amatsutsa malangizo a m’Baibulo pa nkhaniyi. Iwo amaganiza kuti kuona anthu ena kuti ndi okuposani kungachititse kuti anthuwo azikupezererani. Koma kodi zotsatira za maganizo a anthu odzikonda a m’dzikoli ndi zotani? Kodi anthu odzikonda amakhala osangalala? Kodi amakhala ndi mabanja osangalala komanso anzawo enieni? Nanga amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu? Kodi mumaona kuti chothandiza n’chiyani pakati pa kutsatira nzeru za anthu a m’dzikoli ndi kutsatira nzeru za m’Mawu a Mulungu? (1 Akor. 3:19) Anthu amene amatsatira malangizo a anthu omwe dzikoli limawaona kuti ndi anzeru sizingawayendere bwino. Amakhala ngati mlendo yemwe akufunsa mlendo mnzake njira, pomwe awiri onsewo asochera. Yesu ananena za anthu omwe ankaoneka kuti ndi anzeru pa nthawi yake kuti: “Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.” (Mat. 15:14) Kunena zoona, nzeru za m’dzikoli ndi zopusa kwa Mulungu. w19.05 24-25 ¶14-16
Lachiwiri, November 2
Adzasonkhanitsa osankhidwa ake.—Mat. 24:31.
Posachedwapa, chiwerengero cha anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso chakhala chikuwonjezereka. Kodi tiyenera kudandaula ndi zimenezi? Ayi. “Yehova amadziwa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Mosiyana ndi Yehova, abale amene amawerenga anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso sadziwa amene adzozedwadi. Choncho pa chiwerengerochi pamakhalanso anthu amene amangoganiza kuti ndi odzozedwa koma asanadzozedwe. Ndipo pali Akhristu ena amene poyamba ankadya zizindikiro koma anasiya. Ena akhoza kukhala ndi matenda a maganizo amene amawachititsa kuganiza kuti adzakalamulira ndi Khristu kumwamba. Kunena zoona, sitidziwa chiwerengero chenicheni cha odzozedwa amene ali padziko lapansili. Padzakhala odzozedwa m’mayiko ambiri Yesu akamadzabwera kudzawatenga. Baibulo limasonyeza kuti m’masiku otsiriza, padzatsala odzozedwa ena ochepa padzikoli. (Chiv. 12:17) Koma silimatchula chiwerengero cha odzozedwa amene adzakhale adakali padzikoli chisautso chachikulu chikamadzayamba. w20.01 29-30 ¶11-13
Lachitatu, November 3
Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.—Yoh. 3:16.
Yesu anapereka fanizo la mwana wolowerera pofuna kutithandiza kumvetsa mmene Yehova amatikondera. (Luka 15:11-32) Bambo wamufanizoli sanasiye kuyembekezera kuti mwana wake adzabwerera. Ndipo mwanayo atabwerera, iwo anamulandira bwino. Ngati ifenso talakwitsa zinazake koma talapa, tisamakayikire kuti Yehova, yemwe ndi Atate wathu wachikondi, ndi wokonzeka ndiponso wofunitsitsa kutilandiranso. Atate wathu adzathetsa mavuto onse amene Adamu anayambitsa. Adamu atachimwa, Yehova anakonza zoti adzatenge anthu 144,000 padzikoli kuti akakhale mafumu komanso ansembe limodzi ndi Yesu kumwamba. M’dziko latsopano, Yesu ndi odzozedwa adzathandiza anthu omvera kuti akhale angwiro. Akadzapulumuka pa mayesero omaliza, Mulungu adzapereka moyo wosatha kwa anthuwo. Pa nthawi imeneyo, Yehova adzasangalala kuona kuti dziko lonse ladzaza ndi ana ake angwiro. Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri. w20.02 6-7 ¶17-19
Lachinayi, November 4
Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.—Aef. 4:23.
Aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi munthune ndangosintha pamwambamwamba kapena ndasinthadi kuchokera mumtima?’ Funso limeneli ndi lofunika kwambiri. Yesu ananena zimene tiyenera kuchita pa Mateyu 12:43-45. Mfundo yaikulu palembali ndi yakuti: Tikachotsa zinthu zolakwika m’maganizo athu, tiyenera kuikamo maganizo a Mulungu. Kodi n’zothekadi kusintha kuchokera mumtima? Mawu a Mulungu amanena kuti: ‘Muvale umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.’ (Aef. 4:24) Apa zikuoneka kuti n’zotheka kusintha kuchokera mumtima koma si zophweka. Kungodziletsa kuti tisachite kapena kulakalaka zinthu zina si kokwanira. Tiyenera kusintha “mphamvu yoyendetsa maganizo” athu. Apa tikutanthauza kuti tiyenera kusintha mtima wathu, zimene timalakalaka komanso zimene tinazolowera kuchita. Kuti zimenezi zitheke, pamafunika kuchita khama nthawi zonse. w19.06 9-10 ¶6-7
Lachisanu, November 5
Malo ano tiwawononga.—Gen. 19:13.
Yehova anachitira chifundo Loti n’kutumiza angelo kuti akamupulumutse limodzi ndi banja lake. Koma Loti ‘ankazengereza.’ Choncho angelowo anamugwira dzanja n’kumuthandiza kuti athawe limodzi ndi banja lake. (Gen. 19:15, 16) Angelowo anamuuza kuti athawire kumapiri. Koma m’malo mongomvera Yehova, Loti anapempha kuti apite kutauni ina yapafupi. (Gen. 19:17-20) Yehova anamulezera mtima ndipo anamulola kuti apite kutauni imeneyo. Koma kenako Loti anayamba kuopa kukhala m’tauniyi ndipo anasamukira kumapiri kumene Yehova anamuuza kuti apite kuja. (Gen. 19:30) Apatu Yehova anasonyeza kuleza mtima kwambiri. Mofanana ndi Loti, Mkhristu mnzathu akhoza kusankha zinthu mopanda nzeru n’kukumana ndi mavuto. Kodi mungatani zimenezi zitachitika? Mwina tingafune kungomuuza zoona kuti akukolola zimene anafesa. (Agal. 6:7) Koma tingachite bwino kutsanzira mmene Yehova anathandizira Loti. w19.06 20- 21 ¶3-5
Loweruka, November 6
Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.—Aheb. 13:6.
Adani athu akamatiletsa kulambira Yehova amaganiza kuti tichita mantha n’kusiyadi. Iwo akhozanso kufalitsa mabodza okhudza ifeyo, kutumiza apolisi kuti afufuze zinthu m’nyumba zathu, kutitengera kukhoti kapenanso kutsekera ena kundende. Iwo amaganiza kuti tikhoza kuchita mantha kwambiri chifukwa choti anzathu ochepa ali kundende. Koma tikangoyamba kuchita mantha, tikhoza kubwerera m’mbuyo n’kukhala ngati tadzipatsa tokha bani pa kulambira kwathu. Si bwino kukhala ngati anthu ofotokozedwa pa Levitiko 26:36, 37. Sitingalole kuchita mantha mpaka kufika pochepetsa kapena kusiyiratu zimene timachita polambira Yehova. Timadalira Yehova ndi mtima wonse ndipo sitida nkhawa kwambiri. (Yes. 28:16) Timamupempha kuti azititsogolera. Ndipo timadziwa kuti ngati ali kumbali yathu, ngakhale boma lamphamvu kwambiri silingatilepheretse kumulambira mokhulupirika. Adani athu akamatitsutsa zingapangitse kuti tizitumikira Yehova kwambiri m’malo motichititsa mantha. w19.07 9-10 ¶6-7
Lamlungu, November 7
Lalikira mawu.—2 Tim 4:2.
Musataye mtima ngati mukuvutika kupeza munthu woti muziphunzira naye Baibulo. Musaiwale kuti Yesu anayerekezera ntchito yothandiza anthu kukhala ophunzira ndi ntchito yopha nsomba. Asodzi amatha kugwira ntchito kwa nthawi yaitali asanapeze nsomba. Nthawi zambiri amagwira ntchito usiku kapena m’bandakucha ndipo nthawi zina amayenda mtunda wautali kuti akapeze nsomba. (Luka 5:5) Nawonso Akhristu amakhala oleza mtima ndipo amagwira ntchito yolalikira kwa maola ambiri. Iwo amatha kusinthasintha nthawi komanso malo pofufuza anthu. Amatero n’cholinga choti akumane ndi anthu ambiri. Akhristu amene amachita khama, nthawi zambiri amapeza anthu amene amachita chidwi ndi uthenga wathu. Mwina inunso mungasinthe nthawi yolalikira kapena malo kuti muzipeza anthu ambiri. (2 Tim. 4:1, 2) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima tikamaphunzira Baibulo ndi munthu? Chifukwa chimodzi n’chakuti timafunika kuchita zambiri, osati kungothandiza munthuyo kuti adziwe ndiponso kukonda mfundo za m’Baibulo. Timafunikanso kuthandiza munthuyo kuti adziwe ndiponso kukonda Yehova, yemwe analemba Baibulo. w19.07 18-19 ¶14-15
Lolemba, November 8
Ndikuiwala zinthu zakumbuyo.—Afil. 3:13.
Enafe timafunika kusiya kudziimba mlandu pa zinthu zimene tinalakwitsa m’mbuyomu. Kuti tisiye kudziimba mlandu, tingachite bwino kuphunzira mozama nkhani ya dipo la Khristu. Kuphunzira, kuganizira mozama komanso kupempherera nkhani ya dipoyi kungatithandize kuti tisiye kudziimba mlandu kwambiri. Ndipo mwina tikhoza kusiyiratu kudzizunza chifukwa cha machimo amene Yehova anakhululuka kale. Kodi n’chiyaninso chimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Paulo? Anthu ena mwina anasiya ntchito yapamwamba n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Mulungu. Ngati ndi choncho, tikhoza kuiwala zinthu zakumbuyo popewa kulakalaka zinthu zimene tikuganiza kuti tikanazipeza tikanakhala kuti tikugwirabe ntchitoyo. (Num. 11:4-6; Mlal. 7:10) “Zinthu zakumbuyo” zikhozanso kukhala zimene tinakwanitsa kuchita kapena mavuto amene tinapirira. N’zoona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kulimba ngati titaganizira mmene iye wakhala akutidalitsira kapena mmene watithandizira m’mbuyomu. Koma si bwino kungokhutira ndi zimenezo n’kumaganiza kuti tachita zokwanira.—1 Akor. 15:58. w19.08 3 ¶5-6
Lachiwiri, November 9
Muzipemphera mosalekeza.—1 Ates. 5:17.
Tikhoza kupemphera kwa Mulungu wathu nthawi iliyonse komanso malo alionse. Iye amakhala wokonzeka kumvetsera mapemphero athu nthawi ina iliyonse. Tikazindikira kuti Yehova amamvetsera mapemphero athu timamukonda kwambiri. M’pake kuti wolemba masalimo ananena kuti: “Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva Mawu anga.” (Sal. 116:1) Si kuti Yehova amangomva mapemphero athu, koma amayankhanso. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chilichonse chimene tingamupemphe [Mulungu] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yoh. 5:14, 15) N’zoona kuti mwina Yehova sangayankhe mapemphero athu m’njira imene ifeyo tikuganizira. Iye amadziwa bwino zimene tikufunikira choncho nthawi zina sangatipatse zimene tikupempha kapena angafune kuti tidikire kaye. (2 Akor. 12:7-9) Yehova amatipatsa zinthu zofunika. Iye amachita zimene amafuna kuti bambo aliyense azichita. (1 Tim. 5:8) Mwachitsanzo, amapatsa ana ake zofunika pa moyo. Safuna kuti tizidera nkhawa za chakudya, zovala ndi malo ogona. (Mat. 6:32, 33; 7:11) Popeza ndi Atate wachikondi, iye wakonza zoti tizidzapeza zinthu zonse zofunika m’tsogolo. w20.02 5 ¶10-12
Lachitatu, November 10
Zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.—Yoh. 10:16.
Si onse amene akuyembekezera kupita kumwamba omwe ali m’gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Mofanana ndi nthawi ya atumwi, masiku ano Yehova ndi Yesu akugwiritsa ntchito abale ochepa kuti azidyetsa, kapena kuti kuphunzitsa, anthu ambiri. M’nthawi ya atumwi, Akhristu odzozedwa ochepa okha ndi amene anagwiritsidwa ntchito kulemba Malemba a Chigiriki. Masiku anonso, Akhristu odzozedwa ochepa okha ndi amene ali ndi udindo wopatsa anthu a Mulungu “chakudya pa nthawi yoyenera.” Yehova anasankha kuti anthu ake ambiri adzakhale ndi moyo wosatha padzikoli ndipo ochepa adzakalamulire ndi Yesu kumwamba. Yehova amadalitsa atumiki ake onse, kaya ali m’gulu la “Myuda” kapena la “amuna 10.” (Zek. 8:23) Ndipo amafuna kuti onse azimvera malamulo ake komanso kukhalabe okhulupirika. Onse amafunikanso kukhala odzichepetsa, kutumikira Yehova limodzi komanso kukhala ogwirizana. Ayeneranso kuyesetsa kuti mumpingo muzikhalabe mtendere. Pamene mapeto akuyandikira, tiyeni tonse tizitumikira Yehova komanso kutsatira Khristu monga “gulu limodzi.” w20.01 31 ¶15-16
Lachinayi, November 11
Ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma . . . poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.—1 Pet. 3:1, 2.
Sitingakakamize achibale athu kuti azimvetsera uthenga wabwino. Koma tikhoza kuwathandiza kuti akhale ndi mtima wofuna kumvetsera uthengawu. (2 Tim. 3:14, 15) Muzikhala ndi khalidwe labwino. Nthawi zambiri, zochita zathu n’zimene zimathandiza kwambiri achibale athu kuposa zolankhula zathu. Musagwe ulesi pothandiza achibale anu. Yehova wapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye amapereka mpata kwa anthu “mobwerezabwereza” kuti amvetsere uthenga wabwino n’cholinga choti adzapulumuke. (2 Mbiri 36:15) Nayenso mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti asasiye kuthandiza anthu ena. Ananena kuti akamachita zimenezi adzadzipulumutsa yekha komanso anthu amene angamumvere. (1 Tim. 4:16) Timakonda achibale athu choncho timafuna kuti adziwe choonadi. w19.08 14 ¶2; 16-17 ¶8-9
Lachisanu, November 12
Kudzudzula munthu mosabisa mawu, kuli bwino kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza chikondicho.—Miy. 27:5.
Tizikumbukira kuti ngati munthu wafika potipatsa malangizo, ndiye kuti talakwitsa kwambiri kuposa mmene tikuganizira. Mwina poyamba tingaganize kuti sitikufunikira malangizowo. Ndipo tingayambe kupezera zifukwa munthu amene watipatsa malangizowo kapena mmene anawaperekera. Koma ngati ndife odzichepetsa tingayesetse kuona zinthu moyenera. Munthu wodzichepetsa amayamikira akapatsidwa malangizo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti muli kumisonkhano. Ndiye mutacheza ndi abale ndi alongo angapo, munthu wina akukutengerani pambali n’kukuuzani kuti kachakudya kenakake katsalira m’mano. N’zosachita kufunsa kuti mungachite manyazi. Koma mungayamikire kuti wakuuzani zimenezo ndipo mwina mukanakonda ngati wina akanakuuzani mwamsanga. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kudzichepetsa n’kumayamikira ngati Mkhristu mnzathu walimba mtima n’kutipatsa malangizo. Tiyenera kuona kuti munthuyo ndi mnzathu osati mdani wathu.—Miy. 27:5, 6; Agal. 4:16. w19.09 5 ¶11-12
Loweruka, November 13
Mwana wanga, sunga lamulo la bambo ako, ndipo usasiye malangizo a mayi ako.—Miy. 6:20.
Yehova wapatsa amayi udindo wolemekezeka m’banja ndipo iwo ayeneranso kuyang’anira ana awo. Kunena zoona, zimene mayi amachita zimakhudza kwambiri moyo wa ana. (Miy. 22:6) Tiyeni tsopano tione zimene amayi angaphunzire kwa Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu. Mariya ankadziwa bwino Malemba. Iye ankalemekezanso kwambiri Yehova ndipo anali naye pa ubwenzi wolimba. Iye anali ndi mtima wofuna kuchita zimene Yehova ankafuna ngakhale kuti zimenezi zinasinthiratu moyo wake. (Luka 1:35-38, 46-55) Ngati ndinu amayi, kodi mungatsanzire bwanji Mariya? Choyamba, muyenera kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mungachite zimenezi pophunzira Baibulo komanso kupemphera panokha. Chachiwiri, muyenera kulolera kusintha zinthu zina pa moyo wanu kuti musangalatse Yehova. w19.09 18 ¶17-19
Lamlungu, November 14
Nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu.—Chiv. 7:9.
Mtumwi Yohane anaona masomphenya a zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolo. M’masomphenyawo, angelo anauzidwa kuti agwire mphepo zowononga za chisautso chachikulu kufikira akapolo ena atadindidwa chidindo chomaliza. (Chiv. 7:1-3) Akapolowo ndi anthu okwana 144,000 omwe adzalamulire ndi Yesu kumwamba. (Luka 12:32; Chiv. 7:4) Kenako Yohane anatchulanso za gulu lina lalikulu kwambiri moti ananena kuti: “Ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse. Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:9-14) Yohane ayenera kuti anasangalala kwambiri atadziwa kuti m’tsogolo anthu ambirimbiri azidzalambira Mulungu woona. N’zosakayikitsa kuti chikhulupiriro cha Yohane chinalimba ataona masomphenyawa. Masomphenyawa akhoza kulimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu chifukwa tikukhala mu nthawi imene akukwaniritsidwa. Masiku ano anthu ambirimbiri akusonkhanitsidwa ndipo akuyembekezera kupulumuka pa chisautso chachikulu n’kudzakhala padzikoli mpaka kalekale. w19.09 26 ¶2-3
Lolemba, November 15
Chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo . . . ndipo sadzapulumuka.—1 Ates. 5:3.
Tangoyerekezerani kuti maboma alengeza zimene takhala tikuziyembekezera kwa nthawi yaitali zakuti “bata ndi mtendere.” Mwina alengezanso kuti akwanitsa kubweretsa mtendere padziko lonse. Pa nthawiyo, maboma adzafuna kuti tiziganiza kuti apeza njira yothetsera mavuto amene anthu akukumana nawo. Koma zoona zake n’zakuti sadzakhala ndi mphamvu zoti asinthe zimene zidzachitike pambuyo pake. “Babulo Wamkulu” adzawonongedwa. (Chiv. 17:5, 15-18) ‘Mulungu adzaika m’mitima yawo kuti achite mogwirizana ndi maganizo ake.’ Maganizo amenewa ndi akuti awononge zipembedzo zonse zonyenga, kuphatikizapo matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Mulungu adzaika maganizo akewa m’mitima ya “nyanga 10” za ‘chilombo chofiira.’ Nyanga 10 zikuimira maboma onse amene amathandiza “chilombocho,” chomwe ndi bungwe la United Nations. (Chiv. 17:3, 11-13; 18:8) Mabomawa akadzayamba kuukira zipembedzo zonyenga, chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu. Zimenezi zidzakhala zoopsa kwambiri padziko lonse lapansi. w19.10 14 ¶1, 3
Lachiwiri, November 16
Diotirefe, amene amakonda kukhala woyamba pakati pawo, salandira mwaulemu chilichonse chochokera kwa ife.—3 Yoh. 9.
Nthawi ya atumwi, Diotirefe ankachitira nsanje anthu amene ankatsogolera mumpingo. Iye ankafuna “kukhala woyamba” pakati pa Akhristu, choncho ankanenera zamwano mtumwi Yohane ndi abale ena amene ankatsogolera n’cholinga choti aipitse mbiri yawo. (3 Yoh. 10) Mwina sitingafike pochita zinthu ngati Diotirefe koma tikhoza kuyamba kuchitira nsanje anthu amene apatsidwa utumiki umene timaulakalaka, makamaka ngati tikuona kuti nafenso ndi oyenera kulandira utumikiwo. Nsanje ili ngati chomera choipa kwambiri. Ikangozika mizu mumtima mwathu zimakhala zovuta kwambiri kuti tiichotse. Ndipo imakula chifukwa cha makhalidwe ena oipa monga kusirira, kudzikuza ndi kudzikonda. Nsanje ikhoza kulepheretsa munthu kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chifundo ndi kukoma mtima. Choncho tikangozindikira kuti tayamba kamtima ka nsanje tiyenera kukachotseratu. w20.02 15 ¶6-7
Lachitatu, November 17
Ndinapatsidwa munga m’thupi.—2 Akor. 12:7.
Paulo ankatanthauza kuti anali ndi vuto linalake limene linkamusowetsa mtendere kwambiri. Pofotokoza za vutoli, iye anati linali ngati “mngelo wa Satana” amene ‘ankamumenya nthawi zonse.’ Satana kapena ziwanda ayenera kuti si amene anayambitsa mavuto a Paulo mwachindunji ngati kuti ankatenga minga n’kumamubaya. Koma mwina iwo ataona mungawo, kapena kuti vuto lakelo, ankafunitsitsa kuukanikizira mkati kuti uzimupweteka kwambiri. Ndiye kodi Paulo anatani? Poyamba, Paulo ankafuna kuti Yehova achotse ‘mungawo.’ Iye ananena kuti: “Katatu konse ndinachonderera Ambuye [Yehova] kuti mungawu undichoke.” Koma mungawo sunachokebe. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sanayankhe mapemphero a Paulo? Ayi, anayankha. Kungoti sanachotse mungawo koma anamupatsa mphamvu kuti azipirira. Yehova ananena kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.” (2 Akor. 12:8, 9) Mothandizidwa ndi Mulungu, Paulo anakwanitsa kukhalabe ndi mtendere wamumtima komanso kukhala wosangalala.—Afil. 4:4-7. w19.11 9 ¶4-5
Lachinayi, November 18
Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.—Nah. 1:2.
Tiyenera kukhala odzipereka kwa Yehova yekha chifukwa chakuti ndi amene anatilenga komanso kutipatsa moyo. (Chiv. 4:11) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Ngakhale kuti timakonda Yehova komanso kumulemekeza, zinthu zina zikhoza kutilepheretsa kukhala odzipereka kwa iye yekha. M’Baibulo, mawu akuti kudzipereka kwa Mulungu amatanthauza kumukonda ndi mtima wonse. Munthu wodzipereka kwa Yehova yekha amalambira iyeyo basi. Ndipo salola kuti munthu wina kapena chinthu china chizikhala pamalo oyamba. (Eks. 34:14) Si kuti timangokhala odzipereka kwa Yehova m’chimbulimbuli. Tikutero chifukwa timadzipereka pambuyo pophunzira zinthu zokhudza iyeyo komanso kukonda makhalidwe ake. Timadziwa zimene amakonda ndi zimene amadana nazo ndipo timagwirizana ndi maganizo ake. Timadziwanso cholinga chimene anatilengera ndipo timaona kuti n’chabwino. Ndipo timayamikira kuti watipatsa mwayi wokhala anzake. (Sal. 25:14) Chilichonse chimene timaphunzira chokhudza Mlengi wathuyu chimatithandiza kuti tizimukonda kwambiri.—Yak. 4:8. w19.10 26 ¶1-3
Lachisanu, November 19
Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Masiku ano, abale ndi alongo athu amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, amakumana ndi ngozi zachilengedwe komanso zoyambitsidwa ndi anthu. Zimenezi zikachitika, mwina tingalolere kuti abale athuwo adzakhale kunyumba kwathu. Apo ayi, tingawathandize ndi ndalama. Koma aliyense angapemphe Yehova kuti azithandiza abale ndi alongowo. Tikamva kuti m’bale kapena mlongo wina akuvutika maganizo, tikhoza kusowa chonena kapena chochita. Koma mfundo ndi yakuti aliyense wa ife angathandize anzake m’njira inayake. Mwachitsanzo, tingapeze mpata wocheza nawo ndipo akamalankhula, tiziwamvetsera mwachifundo. Tingawauzenso malemba amene amatilimbikitsa kwambiri. (Yes. 50:4) Chofunika kwambiri ndi kukhala limodzi ndi anzathu pamene akukumana ndi mavuto. Tiyenera kuyesetsa panopa kuti tizigwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo athu. Ndipo sitidzasiya kugwirizana komanso kukondana mpaka kalekale. w19.11 7 ¶18-19
Loweruka, November 20
[Lamuloli ndi] la nsembe yachiyanjano imene aliyense azipereka kwa Yehova.—Lev. 7:11.
Munthu ankasankha yekha kupereka nsembe imeneyi chifukwa chokonda Yehova Mulungu. Munthuyo ankadya nyama imene wapereka nsembeyo limodzi ndi banja lake komanso ansembe. Koma mbali zina za nyamayo ankazipereka kwa Yehova basi. Yehova ankaona kuti mafuta ndi mbali yabwino kwambiri ya nyama. Ananenanso kuti ziwalo zina monga impso zinali zamtengo wapatali. (Lev. 3:6, 12, 14-16) Choncho Yehova ankasangalala kwambiri Aisiraeli akapereka mwa kufuna kwawo mafuta kapena ziwalo ngati zimenezi. Ndipo munthu amene wapereka zimenezi ankasonyeza kuti akufunitsitsa kupatsa Mulungu zinthu zake zamtengo wapatali. Nayenso Yesu anapereka zinthu zake zabwino kwambiri kwa Yehova. Anachita zimenezi pomutumikira ndi mtima wake wonse chifukwa chomukonda. (Yoh. 14:31) Yesu ankasangalala kuchita zimene Mulungu ankafuna. (Sal. 40:8) Yehova ayenera kuti ankasangalala kwambiri kuona Yesu akumutumikira ndi mtima wonse. w19.11 22-23 ¶9-10
Lamlungu, November 21
Tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse. Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova.—Eks. 31:15.
Mawu a Mulungu amasonyeza kuti pambuyo polenga zinthu kwa ‘masiku 6,’ Mulungu anapuma pa ntchito yake yolenga zinthu padzikoli. (Gen. 2:2) Koma Yehova amakonda kugwira ntchito ndipo “akugwirabe ntchito” zina mpaka pano. (Yoh. 5:17) Iye anagwira ntchito kwa ‘masiku 6’ n’kupuma la 7 ndipo anauza Aisiraeli kuti azipumanso pa tsiku la 7. Mulungu ananena kuti Sabata linali chizindikiro pakati pa iye ndi Aisiraeliwo. (Eks. 31:12-14) Aliyense sankayenera kugwira ntchito, kaya ndi mwana, kapolo kapena ziweto. (Eks. 20:10) Tsikuli linkathandiza kuti anthu azichita zinthu zokhudza kulambira Mulungu. Koma atsogoleri achipembedzo a nthawi ya Yesu anaika malamulo okhwima okhudza tsikuli. Ankanena kuti n’kulakwa ngakhale kungobudula ngala za mbewu pa tsikuli kapena kuchiritsa munthu amene akudwala. (Maliko 2:23-27; 3:2-5) Zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi maganizo a Yehova ndipo Yesu anathandiza anthu kuzindikira mfundoyi. w19.12 3-4 ¶8-9
Lolemba, November 22
Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.—Aef. 5:1.
Tikamaphunzira kwambiri za makhalidwe a Yehova m’pamene tingathe kumutsanzira bwino. Davide ankadziwa bwino Atate wake wakumwamba choncho zinali zosavuta kuti azimutsanzira pochita zinthu ndi anthu ena. Popeza Davide anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, Aisiraeli ankamukonda kwambiri ndipo Yehova ankaona kuti iye ndi chitsanzo chabwino kwa mafumu ena onse. (Maf. 15:11; 2 Maf. 14:1-3) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Tiyenera kuyesetsa ‘kutsanzira Mulungu.’ Tikamatsanzira Yehova timasonyeza kuti ndifedi ana ake. (Aef 4:24) Anthufe tidzaphunzira za Yehova mpaka kalekale. (Mlal. 3:11) Chofunika si kungodziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova koma kugwiritsa ntchito bwino zimene tikudziwazo. Tikamachita zimenezi komanso kutsanzira Atate wathu, tidzapitiriza kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Yak. 4:8) Yehova amatitsimikizira m’Mawu ake kuti sadzasiya anthu amene amayesetsa kumudziwa. w19.12 20 ¶20; 21 ¶21, 23
Lachiwiri, November 23
Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse.—Yer. 17:9.
Yakobo ankakonda ana ake onse, koma ankakonda kwambiri mwana wake wazaka 17 dzina lake Yosefe. Kodi abale ake a Yosefe anatani? Iwo ankamuchitira nsanje ndipo zimenezi zinachititsa kuti ayambe kumuda. Choncho anamugulitsa kuti akhale kapolo n’kukanamiza bambo awo kuti waphedwa ndi chilombo cholusa. Nsanje inawachititsa kuti asokoneze mtendere wa banja lonse komanso amvetse chisoni kwambiri bambo awo. (Gen. 37:3, 4, 27-34) Nsanje ili m’gulu la “ntchito za thupi” zimene zingachititse kuti munthu asadzalowe mu Ufumu wa Mulungu. (Agal. 5:19-21) Ndipo nsanje ndi imene imayambitsa mavuto ena monga udani, ndewu ndi kupsa mtima. Zimene abale ake a Yosefe anachita zimasonyeza mmene nsanje ingasokonezere ubwenzi wa anthu komanso mtendere m’banja. N’zoona kuti sitingachite zimene abale ake a Yosefe anachita, koma tonsefe si angwiro ndipo tili ndi mtima wonyenga. Choncho n’zosadabwitsa kuti nthawi zina tingalimbane ndi kamtima kansanje. w20.02 14 ¶1-3
Lachitatu, November 24
Modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.
Pa nthawi ina Yehova anachotsa mphamvu ina ya mzimu woyera kwa Mose n’kuipereka kwa akulu ena a Chiisiraeli omwe ankaima pafupi ndi chihema chokumanako. Kenako Mose anamva kuti akulu awiri amene sanapite kuchihemacho analandiranso mzimu woyera ndipo anayamba kuchita zinthu ngati aneneri. Kodi iye anatani Yoswa atamuuza kuti awaletse akuluwo? Mose ataona kuti Yehova akugwiritsa ntchito akulu awiriwo sanawachitire nsanje. M’malomwake, iye anasonyeza kudzichepetsa ndipo anasangalala nawo chifukwa cha udindo umene anapatsidwa. (Num. 11:24-29) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mose? Ngati ndinu mkulu, kodi munapemphedwapo kuti muphunzitse munthu wina kuti azichita utumiki umene mumaukonda kwambiri? Ngati ndinu wodzichepetsa ngati Mose, simungadandaule ngati mwapemphedwa kuphunzitsa m’bale wina. M’malomwake, mudzasangalala kuthandiza m’bale wanuyo. w20.02 15 ¶9; 17 ¶10-11
Lachinayi, November 25
Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.—Miy. 12:25.
Tikadwala tikhoza kukhumudwa n’kumaona kuti sitingachite chilichonse potumikira Yehova. Tikhozanso kuchita manyazi anthu ena akaona kuti tikulephera kuchita zinthu zina kapena tikudalira anzathu kuti azitithandiza. Ngakhale pamene ena sadziwa za matenda athu, tikhoza kuchita manyazi chifukwa choti sitingakwanitse kuchita zinthu zina. Koma Yehova amatilimbikitsa pa nthawi yovuta ngati imeneyi. Kodi amatilimbikitsa bwanji? M’Baibulo muli mawu abwino ambiri amene amatikumbutsa kuti Yehova amatikonda ngakhale kuti tikudwala. (Sal. 31:19; 41:3) Tikamawerenga mawuwo, Yehova adzatithandiza kuti tisamadzione ngati achabechabe tikamadwala. Dziwani kuti Yehova amamvetsa mavuto anu. Choncho muzimupempha kuti azikuthandizani kukhala ndi maganizo oyenera. Muziwerenganso mawu abwino amene Yehova wakusungirani m’Baibulo. Muziganizira kwambiri malemba amene amasonyeza kuti Yehova amakonda atumiki ake. Mukamachita zimenezi, mudzaona kuti Yehova amakomera mtima anthu onse amene amamutumikira mokhulupirika.—Sal. 84:11. w20.01 15-16 ¶9-10; 17 ¶12
Lachisanu, November 26
Usamatsanzire zinthu zoipa koma uzitsanzira zabwino.—3 Yoh. 11.
Isaki anali ndi chuma ndipo Afilisiti ankamuchitira nsanje. (Gen. 26:12-14) Iwo anafika pokwirira zitsime zake zomwe ankagwiritsa ntchito pomwetsera ziweto. (Gen. 26:15, 16, 27) Mofanana ndi Afilisiti, anthu ena masiku ano amachitira nsanje anthu amene ali ndi chuma chambiri. Si kuti amangosirira zimene ali nazo koma amafunanso kuti asakhale nazo. Atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda ankachitira Yesu nsanje chifukwa choti anthu ambiri ankamukonda. (Mat. 7:28, 29) Yesu ankaimira Mulungu komanso ankaphunzitsa mfundo zachoonadi. Ngakhale zinali choncho, atsogoleriwo ankafalitsa mabodza okhudza Yesu n’cholinga choti aipitse mbiri yake. (Maliko 15:10; Yoh. 11:47, 48;12:12, 13, 19) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? Tiyenera kupewa kamtima kochitira nsanje anthu amene ali ndi makhalidwe omwe amachititsa anthu ambiri mumpingo kuwakonda. M’malomwake, tiziyesetsa kutsanzira makhalidwe awo abwino.—1 Akor. 11:1. w20.02 15 ¶4-5
Loweruka, November 27
Lamuloli ndi lakuti aphedwe.—Esitere 4:11.
Yerekezerani kuti munali ku Perisiya zaka 2,500 zapitazo. Mukufuna kukalankhula ndi mfumu ndipo mukupita kumzinda wa Susani kumene mfumuyo imakhala. Koma musanalankhule ndi mfumuyo mukufunika kupatsidwa chilolezo. Ngati mutangopita mfumuyo isanakupatseni chilolezo, mukhoza kuphedwa. Timayamikira kwambiri kuti Yehova sali ngati mfumu ya ku Perisiya. Iye ndi wamkulu komanso wofunika kwambiri kuposa mfumu iliyonse, koma amatilola kuti tizilankhula naye nthawi iliyonse. Komanso amafuna kuti tizikhala omasuka kulankhula naye. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Yehova ali ndi mayina audindo ngati Mlengi Wamkulu, Wamphamvuyonse komanso Ambuye Wamkulu, iye amafuna kuti tizilankhula naye pogwiritsa ntchito mawu oti “Atate.” (Mat. 6:9) N’zosangalatsa kuti Yehova amafuna kuti tizimva kuti tili naye pa ubwenzi ndipo amatikonda. Yehova ndi amene anatipatsa moyo choncho m’poyenera kumutchula kuti “Atate.” (Sal. 36:9) Popeza ndi Atate wathu, tiyenera kumumvera. Tikamachita zimene iye amafuna, tidzadalitsidwa kwambiri. (Aheb. 12:9) Madalitsowa akuphatikizapo moyo wosatha, kaya ndi kumwamba kapena padzikoli. w20.02 2 ¶1-3
Lamlungu, November 28
Mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga.—Mat. 28:19.
Cholinga chathu ndi kuthandiza anthu kuti akule mwauzimu. (Aef. 4:13) Munthu akavomera kuphunzira, nthawi zambiri amaganizira mmene zinthu zimene akuphunzirazo zingamuthandizire iyeyo. Koma akayamba kukonda kwambiri Yehova, amayambanso kuganizira mmene angathandizire anthu ena, kuphatikizapo amumpingo. (Mat. 22:37-39) Pa nthawi yoyenera, tingamufotokozere kuti tili ndi mwayi wopereka ndalama zothandiza pa ntchito za Ufumu. Muzithandiza anthu kudziwa zimene angachite akakumana ndi mavuto. Tiyerekeze kuti mumaphunzira ndi wofalitsa wosabatizidwa ndipo wakuuzani kuti munthu wina mumpingo wamukhumudwitsa. M’malo moikira kumbuyo munthu mmodzi, mungachite bwino kumufotokozera zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Paja limasonyeza kuti iye akhoza kungomukhululukira munthuyo, koma ngati sangakwanitse, akhoza kukambirana naye mwachikondi n’cholinga choti agwirizane. (Yerekezerani ndi Mateyu 18:15.) Muzimuthandiza kuti akonzekere zimene angakanene pokambirana ndi munthuyo. w20.01 5-6 ¶14-15
Lolemba, November 29
Ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa. . . . Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.—Sal. 32:5.
Timasonyeza kuti timayamikira chifundo cha Yehova tikamapemphera kuti atikhululukire, kuvomereza chilango chimene tapatsidwa komanso tikamayesetsa kuti tisabwereze machimo athu. Tikamachita zimenezi tidzapezanso mtendere wamumtima. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa. (Sal. 34:18) Pamene mapeto akuyandikira, nkhawa zathu zikhoza kumawonjezereka. Mukamada nkhawa muyenera kupempha Yehova mwamsanga kuti akuthandizeni. Muyeneranso kuphunzira Baibulo mwakhama. Muzitengera chitsanzo cha Hana, Mtumwi Paulo ndi Mfumu Davide. Muzipemphanso Atate wanu wakumwamba kuti akuthandizeni kudziwa zimene zikukuchititsani kuda nkhawa. (Sal. 139:23) Muzimulola kuti asenze mavuto anu, makamaka ngati palibe zimene mungachite kuti muwathetse. Mukatero, mukhoza kufanana ndi wolemba masalimo amene anaimbira Yehova kuti: “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”—Sal. 94:19. w20.02 24 ¶17; 25 ¶20-21
Lachiwiri, November 30
Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.—2 Tim. 3:16.
Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “anauziridwa ndi Mulungu” amatanthauza kuti “Mulungu anapumira mpweya.” Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake kuti apumire, kapena kuti aike, mawu ake m’maganizo a anthu olemba Baibulo. Tikamawerenga Baibulo komanso kusinkhasinkha zimene tikuwerengazo, malangizo a Mulungu amalowa m’maganizo ndiponso mumtima mwathu. Kenako malangizowo amatithandiza kuti tisinthe n’kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. (Aheb. 4:12) Koma kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri, tiyenera kumapeza nthawi yophunzira Baibulo komanso kuganizira mozama zimene tikuphunzirazo. Tikatero Mawu a Mulungu azititsogolera pa zonse zimene timalankhula komanso kuchita.Tiyeneranso kulambira Mulungu limodzi. (Sal. 22:22) Mzimu wa Yehova umakhala pamisonkhano yathu yachikhristu. (Chiv. 2:29) Tikamasonkhana timapempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera, timaimba nyimbo za Ufumu zokhala ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu komanso timamvetsera malangizo a m’Baibulo omwe amaperekedwa ndi abale amene anaikidwa ndi mzimu woyera. Koma kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri, tizikonzekera misonkhano komanso kuyesetsa kuyankha. w19.11 11 ¶13-14