December
Lachitatu, December 1
Chilichonse chili ndi nthawi yake . . . nthawi yokhala chete.—Mlal. 3:1, 7.
Ngati sitilamulira lilime lathu, pakhoza kukhala mavuto aakulu. Mwachitsanzo, ngati mwakumana ndi m’bale amene amatumikira m’dziko limene muli bani, kodi mumafuna kumufunsa mmene ntchito yathu ikuyendera m’dzikolo? N’kutheka kuti mungakhale ndi zolinga zabwino. Paja anthufe timakondana ndipo timafuna kudziwa mmene zikuyendera pa moyo wa anzathu. Timafunanso tizitchula zinthu zenizeni popempherera abale athu. Koma nthawi imeneyi ndi yofunika kulamulira lilime lathu kuti tikhale chete. Tikamakakamiza m’bale wathu kuti anene zinthu zachinsinsi timasonyeza kuti sitikumuganizira iyeyo komanso abale ndi alongo ena amene akumudalira kuti sangaulule zinthu ngati zimenezo. Ndipo palibe amene angafune kuchita zinthu zimene zingawonjezere mavuto a abale athu m’mayiko amene muli bani.—w20.03 21 ¶11-12
Lachinayi, December 2
Kufa simudzafa ayi.—Gen. 3:4.
Cholinga cha Mulungu sichinali choti anthu azifa. Koma kuti Adamu ndi Hava asafe, anafunika kumvera lamulo losavuta limene Yehova anawapatsa. Anawauza kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:16, 17) Koma kenako, Satana anabwera kudzalankhula ndi Hava mawu amulemba la leroli. N’zomvetsa chisoni kuti Hava anamvera bodzali n’kudya chipatsocho. Kenako mwamuna wake anadyanso. (Gen. 3:6) Izi zinachititsa kuti uchimo ndi imfa zifalikire kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Mogwirizana ndi zimene Mulungu ananena, Adamu ndi Hava anafa. Koma Satana sanasiye kunena mabodza okhudza imfa. Pa nthawi ina, iye anayamba kufalitsa mabodza ena. Bodza lina ndi lakuti munthu akamwalira, thupi ndi limene limafa koma mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo. Kuyambira kalekale, anthu ambiri akhala akukhulupirira bodza limeneli.—1 Tim. 4:1. w19.04 14-15 ¶3-4
Lachisanu, December 3
Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, ndiponso kuona zinthu ngati kamwana.—1 Akor. 13:11.
Ana amakhala asanafike poganiza bwinobwino kapena pozindikira zinthu zoopsa n’kumazipewa. Choncho anthu ogwirira savutika kunyengerera ana. Anthuwo amachititsa ana kukhulupirira mabodza oopsa. Mwachitsanzo, mwanayo angakhulupirire kuti iyeyo ndi amene wachititsa kuti agwiriridwe. Angakhulupirirenso kuti sayenera kuulula zimene zachitika ndipo akaulula palibe munthu amene angazisamale kapena kukhulupirira. Akhoza kukhulupiriranso kuti palibe vuto ngati akuluakulu agonana ndi ana chifukwa ndi njira yongosonyezera chikondi. Mabodza oterewa angasokoneze maganizo a mwana kwa zaka zambiri. Mwanayo akhoza kumaganiza kuti ndi woipa komanso wosayenera kukondedwa kapena kulimbikitsidwa. Apa zikuonekeratu kuti mwana akagwiriridwa amavutika kwa zaka zambiri. Tikukhala m’masiku otsiriza pamene anthu ambiri ndi “osakonda achibale awo” ndipo ‘anthu oipa ndi onyenga akuipiraipirabe.’—2 Tim. 3:1-5, 13. w19.05 15 ¶7-8
Loweruka, December 4
Mukatero mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.—Agal. 6:2.
Kodi Yesu ankaphunzitsa anthu m’njira ziti? Ankawaphunzitsa polankhula nawo. Zimene ankanena zinali zamphamvu chifukwa zinkathandiza anthu kudziwa mfundo zoona zokhudza Mulungu, cholinga cha moyo komanso kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto. (Luka 24:19) Yesu ankaphunzitsanso anthu powapatsa chitsanzo chabwino. Zimene iye ankachita zinkathandiza otsatira ake kudziwa zimene nawonso ayenera kuchita. (Yoh. 13:15) Nanga kodi ankaphunzitsa pa nthawi ziti? Yesu ankaphunzitsa anthu pamene ankachita utumiki wake padzikoli. (Mat. 4:23) Iye anaphunzitsanso otsatira ake atangoukitsidwa kumene. Mwachitsanzo, anaonekera kwa ophunzira, mwina oposa 500, ndipo anawalamula kuti ‘aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.’ (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 15:6) Popeza Yesu ndi mutu wa mpingo, anapitiriza kuphunzitsa ophunzira ake ngakhale atabwerera kumwamba. Mwachitsanzo, cha m’ma 96 C.E., Khristu anagwiritsa ntchito mtumwi Yohane kuti alimbikitse Akhristu odzozedwa ndiponso kuwalangiza.—Akol. 1:18; Chiv. 1:1. w19.05 3 ¶4-5
Lamlungu, December 5
Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.—Afil. 1: 10.
Masiku ano pamafunika khama kuti tizipeza zofunika pa moyo. Abale ambiri amagwira ntchito maola ambiri kuti asamalire mabanja awo. Pomwe ena amayenda mtunda wautali tsiku lililonse kuti akafike kuntchito. Enanso amagwira ntchito zotopetsa kuti apeze zofunika pa moyo. Tsiku likamatha amakhala atatoperatu moti safuna kuphunzira. Ngakhale zili choncho, tiyenera kupeza nthawi yoti tiziphunzira mwakhama Mawu a Mulungu komanso zinthu zina zimene gulu latipatsa. Tiyenera kumaphunzira kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhale wolimba komanso kuti tidzapeze moyo wosatha. (1 Tim. 4:15) Ena amadzuka m’mawa kwambiri tsiku lililonse kuti aziphunzira Mawu a Mulungu pambuyo poti apuma usiku komanso kulibe phokoso. Enanso amapeza maminitsi ochepa madzulo kuti aphunzire Mawu a Mulungu komanso kuganizira zimene aphunzira. w19.05 26 ¶1-2
Lolemba, December 6
Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma 12:2.
Kuti munthu asinthe chonchi, zimatenga nthawi ndipo sizimangochitika zokha. Pangafunike ‘kuyesetsa mwakhama’ kwa zaka zambiri. (2 Pet. 1:5) Chinthu choyamba komanso chofunika kwambiri ndi kupemphera. Tiyenera kupemphera ngati mmene anachitira wolemba masalimo amene ananena kuti: “Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10) Tiyenera kuzindikira kuti tikufunika kusintha mphamvu zoyendetsa maganizo athu ndipo tizipempha Yehova kuti atithandize. Chinthu chachiwiri chofunika ndi kusinkhasinkha. Tikamawerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse tiziganizira mozama zimene tiyenera kusintha m’maganizo ndi mumtima mwathu. (Sal. 119:59; Aheb. 4:12; Yak. 1:25) Tiyenera kuganizira zinthu zimene timachita chifukwa chotengera nzeru zam’dzikoli. Tizizindikira zimene timalakwitsa n’kumayesetsa kusintha. w19.06 8 ¶1; 10 ¶10; 12 ¶11-12
Lachiwiri, December 7
Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.—Aef. 5:16.
Mukamasankha zochita muyenera kusankhanso nthawi imene mudzachitire zimene munasankhazo ndipo musasinthe nthawiyo. Musamadikire nthawi yabwino yoti muchite zinthuzo chifukwa mwina singapezeke. (Mlal. 11:4) Musamalole kuti zinthu zosafunika zizikusokonezani moti n’kusowa nthawi ndi mphamvu zochitira zinthu zofunika kwambiri. (Afil. 1:10) Ngati zingatheke, muzisankha nthawi imene anthu ena sangakusokonezeni. Mungauzenso anthu kuti akupatseni mpata ndipo mungachite bwino kuthimitsa foni komanso kupewa kuona maimelo kapena mameseji. Tingayerekezere kukwaniritsa zimene munasankha ndi kukafika kumalo amene mukupita. Ngati mukufunadi kukafika kumaloko, mumapitirizabe ulendo ndipo ngakhale njira itatsekedwa, mumasintha n’kudzera njira ina. Mofanana ndi zimenezi, tikakhala ndi cholinga chokwaniritsa zimene tinasankha, timayesetsabe kuzikwaniritsa ngakhale titakumana ndi mavuto.—Agal. 6:9. w19.11 30 ¶17-18
Lachitatu, December 8
Mawu a Mulungu . . . amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.—Aheb. 4:12.
Kodi chifukwa chachikulu chokuchititsani kubatizidwa n’chiyani? Pophunzira Baibulo mwadziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova, makhalidwe ake komanso mmene amachitira zinthu. Zimene mwaphunzira zimakusangalatsani ndipo zachititsa kuti muzimukonda kwambiri. Choncho kukonda Yehova kuyenera kukhala chifukwa chachikulu chokuchititsani kuti mubatizidwe. Chifukwa china chokuchititsani kuti mubatizidwe ndi mfundo za m’Baibulo zimene mwaphunzira ndipo mumazikhulupirira. Kumbukirani zimene Yesu ananena polamula anthu kuti azigwira ntchito yophunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20) Yesu ananena kuti munthu ayenera kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Munthu ayenera kukhulupirira ndi mtima wonse mfundo za m’Baibulo zokhudza Yehova, Yesu komanso mzimu woyera. Mfundo zimenezi ndi zamphamvu kwambiri moti zikhoza kukufikani pamtima. w20.03 9 ¶8-9
Lachinayi, December 9
Langizani ochita zosalongosoka, . . . thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.—1 Ates. 5:14.
Yehova anatumiza angelo kuti akachenjeze Loti komanso kuti akamuthandize kutuluka mumzinda wa Sodomu. (Gen. 19:12-14, 17) Ifenso tingafunike kuchenjeza m’bale wathu tikaona kuti akhoza kukumana ndi mavuto. Ndipo tiyenera kumulezera mtima ngati sakutsatira mwamsanga malangizo ochokera m’Baibulo amene wapatsidwa. Tiyenera kutsanzira angelo awiri aja. M’malo motaya mtima n’kungomusiya m’bale wathuyo, tiyenera kuyesetsa kuona mmene tingamuthandizire. (1 Yoh. 3:18) Mwina tiyenera kuchita ngati tamugwira dzanja n’kumuthandiza kuti atsatire malangizo anzeru amene wapatsidwa. Yehova akanatha kumangoganizira zinthu zimene Loti ankalakwitsa. Koma m’malomwake, anauzira mtumwi Petulo kulemba kuti Loti anali munthu wolungama. N’zosangalatsa kwambiri kuti Yehova saganizira kwambiri zimene timalakwitsa. (Sal. 130:3) Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhaniyi? Tikamaganizira kwambiri makhalidwe abwino a abale ndi alongo athu, tikhoza kuwalezera mtima kwambiri. Ndipo iwo sangakane thandizo limene tingawapatse. w19.06 21 ¶6-7
Lachisanu, December 10
Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Ngati boma laletsa ntchito yathu, mukhoza kuganiza kuti, Kodi ndisamukire kudziko lina kuti ndizikalambira Yehova mwaufulu? Palibe munthu amene ayenera kusankhira anzake zochita pa nkhaniyi. Anthu ena angathandizidwe kusankha zochita akaganizira zimene Akhristu oyambirira anachita atayamba kuzunzidwa. Akhristu a ku Yerusalemu anasamukira kumadera ena a ku Yudeya komanso ku Samariya ndipo anapita ngakhale ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. (Mat. 10:23; Mac. 8:1; 11:19) Koma Akhristu atayambiranso kuzunzidwa nthawi ina, mtumwi Paulo anasankha zoti asasamuke kumadera amene anthu ankadana ndi ntchito yolalikira. Anachita izi n’cholinga choti apitirize kulalikira uthenga wabwino ndiponso kulimbikitsa abale amene ankazunzidwa kwambiri. (Mac. 14:19-23) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani zimenezi? Aliyense amene ndi mutu wa banja ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani ya kusamuka. Asanasankhe zochita ayenera kupemphera komanso kuganizira kwambiri mmene zilili ndi banja lake komanso ubwino ndi kuipa kwa kusamuka. Ndipo sitiyenera kuweruza ena chifukwa cha zimene asankha pa nkhaniyi. w19.07 10 ¶8-9
Loweruka, December 11
Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.—Yoh. 17:3.
Yesu ananena kuti “pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:19) Koma kuwonjezera pa kuphunzitsa anthu zimene Yesu amafuna kuti ophunzira ake azichita, tiyenera kuwathandiza moleza mtima kuti ayambe kutsatira mfundo za m’Baibulo. Anthu ena amatha kusintha maganizo ndi makhalidwe awo patangopita miyezi yochepa koma ena zimawatengera nthawi yaitali. Zimene mmishonale wina ku Peru anakumana nazo zimasonyeza kufunika koleza mtima. Iye anati: “Ndinaphunzira mabuku awiri ndi munthu wina dzina lake Raúl. Koma anali adakali ndi mavuto aakulu. Banja lake silinkayenda bwino, ankakonda kutukwana ndipo ana ake sankamulemekeza. Koma ndinapitiriza kumuthandiza limodzi ndi banja lake chifukwa chakuti ankabwera kumisonkhano mlungu uliwonse. Kuchokera pamene ndinakumana naye, panatenga zaka zoposa zitatu kuti ayenerere kubatizidwa.” w19.07 15 ¶3; 19 ¶15-17
Lamlungu, December 12
Yesetsani mwamphamvu.—Luka 13:24.
Taganizirani mmene zinthu zinalili pa moyo wa Paulo pa nthawi imene ankalembera kalata Akhristu a ku Filipi. Iye anali pa ukaidi wosachoka pakhomo ku Roma ndipo analibe ufulu wambiri wolalikira. Koma ankachita khama kulalikira kwa anthu odzamuona komanso kulemba makalata opita kumipingo yakutali. Paulo ankadziwa kuti ayenera kutsanzira Yesu n’kumayesetsa mwamphamvu mpaka mapeto. N’chifukwa chake anayerekezera moyo wa Akhristu ndi mpikisano wothamanga. (1 Akor. 9:24-27) Munthu amene ali pa mpikisano amaganizira kwambiri cholinga chake chokafika kumapeto ndipo salola kuti zinthu zina zimusokoneze. Mwachitsanzo, anthu ochita mpikisano wothamanga masiku ano angamadutse m’misewu yokhala ndi malonda komanso zinthu zina zomwe zingawasokoneze. Ndiye kodi mukuganiza kuti munthu amene ali pa mpikisano angaime kuti aone malonda? Ngati akufuna kupambana pa mpikisanowo, sangachite zimenezi. Ifenso tiyenera kupewa zinthu zimene zingatisokoneze pa mpikisano wokalandira moyo. Tikamaganizira kwambiri cholinga chathu komanso kuyesetsa mwakhama ngati mmene Paulo anachitira, tidzalandira mphoto. w19.08 3 ¶4; 4 ¶7
Lolemba, December 13
Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa. . . . chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.—1 Tim. 4:16.
Tikayamba kutsatira mfundo za Mulungu, achibale athu angavutike kumvetsa zimene timakhulupirira komanso kuchita. Nthawi zambiri, chinthu choyamba chimene amaona n’chakuti tasiya kuchita nawo zandale komanso zikondwerero zachipembedzo. Poyamba, achibale ena angatikwiyire. (Mat. 10:35, 36) Koma sitiyenera kusiya kuwathandiza kuti amvetse zimene timakhulupirira. Tikasiya zingakhale ngati tawaweruza kuti ndi osayenera kudzapeza moyo wosatha. Koma Yehova wapereka udindo woweruzawu kwa Yesu osati ifeyo. (Yoh. 5:22) Tikakhala oleza mtima achibale athu akhoza kuyamba kumvetsera uthenga wathu. Tiyenera kuchita zinthu molimba mtima koma mwaulemu ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. (1 Akor. 4:12b) Mwina zingawatengere nthawi achibale athu kuti amvetse mmene timaonera nkhani yotumikira Yehova. w19.08 17 ¶10, 13; 18 ¶14
Lachiwiri, December 14
Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.—Afil. 4:13.
Mwina ambirife tanenapo kuti, “Pandekha sindikanatha kupirira mavuto amene ndinakumana nawo.” N’kutheka kuti munanena mawu ngati amenewa mutakumana ndi mavuto monga matenda aakulu kapena imfa ya mnzanu. Mwina mumaona kuti munkatha kupirira tsiku lililonse chifukwa choti mzimu woyera wa Yehova unkakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7-9) Timadaliranso mzimu woyera kuti uzitithandiza kupewa zinthu zoipa zam’dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Kuwonjezera pamenepo, tiyenera kulimbana ndi “mizimu yoipa.” (Aef. 6:12) Mzimu wa Yehova umatipatsa mphamvu kuti tikwaniritse maudindo athu ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. Mtumwi Paulo anaona kuti kudalira “mphamvu ya Khristu” ndi kumene kunamuthandiza kuti azitumikirabe Yehova komanso kukwaniritsa utumiki wake ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto.—2 Akor. 12:9. w19.11 8 ¶1-3
Lachitatu, December 15
Amene waona ine waonanso Atate.—Yoh. 14:9.
M’Baibulo muli nkhani zofotokoza bwino zimene Yesu anakuchitirani. Mukamakonda Yesu mudzayambanso kukonda kwambiri Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yesu amatsanzira Atate wake ndendende. Choncho mukadziwa bwino za Yesu mumadziwanso bwino Yehova n’kumamukonda kwambiri. Taganizirani mmene Yesu ankakondera anthu onyozeka monga osauka, odwala komanso amene ankaponderezedwa. Ndiye taganiziraninso malangizo othandiza amene anapereka komanso mmene amatithandizira tikamawatsatira. (Mat. 5:1-11; 7:24-27) Kuganizira nsembe imene Yesu anapereka kuti machimo athu akhululukidwe kungatithandize kuti tizimukonda kwambiri. (Mat. 20:28) Mukazindikira kuti Yesu anadzipereka kuti akufereni, mumafunitsitsa kulapa n’kupempha Yehova kuti akukhululukireni. (Mac. 3:19, 20; 1 Yoh. 1:9) Ndipo mukamakonda Yesu ndi Yehova mumayambanso kukonda anthu ena amene ali nawo pa ubwenzi. w20.03 5-6 ¶10-12
Lachinayi, December 16
Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa.—Sal. 138:6.
M’bale angayambe kuganiza kuti iye ndi amene ali woyenera kwambiri kupatsidwa ntchito inayake. Apo ayi, mlongo angaganize kuti mwamuna wake angachite bwino zinthu zina kuposa abale ena. Koma ngati ndifedi odzichepetsa tidzapewa mtima wodzikuza umenewu. Tingachite bwino kutsanzira zimene Mose anachita anthu ena atalandira udindo. Iye ankaona kuti ntchito yake yotsogolera Aisiraeli inali yamtengo wapatali. Koma kodi Mose anatani Yehova atalola anthu ena kuti azigwira naye ntchito? Iye sanachite nsanje. (Num. 11:24-29) Mose anali wodzichepetsa ndipo analola kuti anthu ena azimuthandiza pa ntchito yoweruza Aisiraeli. (Eks. 18:13-24) Chifukwa cha zimenezi, Aisiraeli ankatha kuthandizidwa mofulumira kuposa kale. Choncho Mose ankaika zofuna za ena pamalo oyamba osati kuganizira kwambiri za udindo wake. Chitsanzo chimenechi ndi chabwino kwambiri kwa ife. Kuti Yehova azitigwiritsa ntchito, chofunika kwambiri ndi kukhala odzichepetsa osati kukhala ndi luso linalake. w19.09 5-6 ¶13-14
Lachisanu, December 17
Yehova amateteza okhulupirika.—Sal. 31:23.
Sitikudziwa zimene maboma adzanene pofotokoza chifukwa chake akuwononga Babulo Wamkulu. Mwina adzanena kuti zipembedzo ndi zimene zikusokoneza mtendere ndipo zimakonda kulowerera ndale. Apo ayi, anganene kuti zipembedzo zili ndi chuma chochuluka kwambiri. (Chiv. 18:3, 7) Zikuoneka kuti powononga zipembedzo si kuti adzawononga anthu onse a m’zipembedzozo. M’malomwake, zikuoneka kuti maboma adzawononga mabungwe a zipembedzozo. Mabungwewo akadzawonongedwa, anthu ake adzazindikira kuti atsogoleri a zipembedzo zonyengazi alephera kuwathandiza. Ndipo n’kutheka kuti anthuwo adzayesetsa kusonyeza kuti sakugwirizana ndi zipembedzozo. Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu sikudzatenga nthawi yaitali. (Chiv. 18:10, 21) Yehova walonjeza kuti ‘adzafupikitsa masiku’ a chisautsocho n’cholinga choti apulumutse ‘osankhidwa’ ake komanso kuti chipembedzo choona chisadzawonongedwe.—Maliko 13:19, 20. w19.10 15 ¶4-5
Loweruka, December 18
Azikumbutsa akazi achitsikana . . . kukonda ana awo.—Tito 2:4.
Ngati ndinu amayi, n’kutheka kuti munaleredwa ndi makolo amtima wapachala omwe ankakonda kukalipira ana. Ndiye inuyo munakula mukuganiza kuti njira yabwino yolerera ana ndi imeneyo. Ndipo ngakhale kuti mwaphunzira mfundo za Yehova, zingakuvutenibe kuugwira mtima makamaka ngati ana anu akuvuta inu mutatopa. (Aef. 4:31) Pa nthawi ngati imeneyo, muyenera kudalira kwambiri Yehova n’kupemphera kwa iye. (Sal. 37:5) Koma amayi ena zimawavuta kuti asonyeze chikondi kwa ana awo. Mwina analeredwa m’banja limene makolo sankasonyeza chikondi kwenikweni kwa ana awo. Ngati inunso munaleredwa m’banja lotere, muziyesetsa kupewa zimene makolo anu ankalakwitsazo. Mayi amene amagonjera Yehova ayenera kuyesetsa kuti azisonyeza chikondi kwa ana ake. N’zoona kuti kusintha kungakhale kovuta. Koma zimenezi n’zotheka ndipo n’zothandiza kwa mayiyo komanso banja lonse. w19.09 18-19 ¶19-20
Lamlungu, December 19
Kapolo sangatumikire ambuye awiri.—Mat. 6:24.
Mtumiki wa Yehova amene amagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake zambiri kuti apeze chuma amakhala ngati akutumikira ambuye awiri. Akatero sangakhale wodzipereka kwa Yehova yekha. Chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, anthu ena mumpingo wa ku Laodikaya ankadzitama kuti: “Ndine wolemera, ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu.” Koma Yehova ndi Yesu ankaona kuti anthuwo anali ‘ovutika, omvetsa chisoni, osauka, akhungu, ndi amaliseche.’ Yesu anawapatsa malangizo poona kuti ankakonda kwambiri chuma moti ubwenzi wawo ndi Yehova unali utayamba kusokonekera. (Chiv. 3:14-17) Choncho tikazindikira kuti tayamba kukonda chuma, tiyenera kusintha nthawi yomweyo. (1 Tim. 6:7, 8) Kupanda kutero, mtima wathu ukhoza kugawanika ndipo Yehova sangasangalale ndi kulambira kwathu. Paja amafuna kuti anthu “azidzipereka kwa iye yekha basi.”—Deut. 4:24. w19.10 27 ¶5-6
Lolemba, December 20
Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.—2 Pet. 1:21.
Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “motsogoleredwa” amatanthauza ‘kutengedwa’ kapena ‘kukankhiridwa kutsogolo.’ Luka, yemwe analemba buku la Machitidwe, anagwiritsanso ntchito mawu a Chigiriki omwewa pofotokoza za ngalawa imene ‘inatengedwa’ ndi mphepo. (Mac. 27:15) Katswiri wina wa mawu a m’Baibulo ananena kuti mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito mawu onena za maulendo apanyanja pofotokoza mmene mzimu woyera unathandizira anthu olemba Baibulo. Apa tingati Petulo ankanena kuti mofanana ndi mmene mphepo imakankhira nsalu za ngalawa kuti ngalawayo ikafike kumene ikupita, mzimu woyera unathandiza olemba Baibulo kuti agwire bwino ntchito yawo. Katswiri uja anati: “Olemba Baibulowo anali ngati ngalawa zimene nsalu zake zothandiza poyenda zakwezedwa.” Yehova anathandiza olembawo powapatsa mzimu wake woyera umene unali ngati mphepo. Ndiyeno olemba Baibulowo anachita mbali yawo polola kutsogoleredwa ndi mzimuwo. Mofanana ndi zimenezi, mzimu woyera ungatithandize kuti tipirire mavuto athu n’kumatumikirabe Yehova mpaka tidzalowe m’dziko latsopano. w19.11 9 ¶7-9
Lachiwiri, December 21
Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.—Miy. 24:10.
Nthawi zina timatha kukhumudwa chifukwa cha mavuto athu. Koma tiyenera kupewa kumangoganizira za mavuto athuwo chifukwa zimenezi zikhoza kutiiwalitsa madalitso amene Yehova walonjeza. (Chiv. 21:3, 4) Ndiye tikhoza kukhumudwa kwambiri mpaka kufooka moti tingafike potaya mtima. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku United States amene akusamalira mwamuna wake yemwe akudwala kwambiri. Iye ananena kuti: “N’zoona kuti vuto lathu limatidetsa nkhawa komanso kutikhumudwitsa nthawi zina, koma chiyembekezo chathu chidakali champhamvu. Ndimayamikira kwambiri zinthu zimene takhala tikulandira zomwe zikutilimbikitsa komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Tinkafunikira kulangizidwa ndi kulimbikitsidwa m’njira imeneyi. Zimatithandiza kuti tizitumikirabe Mulungu n’kumapirira.” Chitsanzo cha mlongoyu chikusonyeza kuti tikhoza kupewa kukhumudwa kwambiri tikakumana ndi mavuto. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kuona kuti mavuto athu ndi njira imene Satana akugwiritsa ntchito potiyesa. Tizikumbukiranso kuti Mulungu ndi amene angatitonthoze. Komanso tiziyamikira chakudya chauzimu chimene amatipatsa. w19.11 16 ¶9-10
Lachitatu, December 22
Wokhulupirika amabisa nkhani.—Miy. 11:13.
Makamaka akulu ayenera kuyesetsa kwambiri kutsatira mfundo ya m’Baibulo imeneyi. Mkulu ayenera kupewa kuulula zinsinsi za abale ndi alongo mumpingo. Kupanda kutero anthu sangamukhulupirire ndipo mbiri yake ikhoza kuipa kwambiri. Paja anthu amene apatsidwa udindo mumpingo ayenera kukhala “osanena pawiri” kapena achinyengo. (1 Tim. 3:8) Apa zikutanthauza kuti ayenera kupewa kupusitsa anzawo kapena kunena miseche. Ngati mkulu amakonda mkazi wake, sangamuuze nkhani zimene safunika kuzidziwa. Akazi a akulu ayenera kupewa kukakamiza amuna awo kuti awauze nkhani zachinsinsi. Mkazi akamapewa zimenezi amathandiza mwamuna wake komanso amasonyeza kuti amalemekeza anthu amene akukhudzidwa ndi nkhani zachinsinsizo. Koma chofunika kwambiri n’chakuti amasangalatsa Yehova chifukwa cholimbikitsa mtendere ndi mgwirizano mumpingo.—Aroma 14:19. w20.03 22 ¶13-14
Lachinayi, December 23
Yehova aonekera ndithu kwa inu.—Lev. 9:4.
Mu 1512 B.C.E. pamene Aisiraeli anaimika chihema m’mphepete mwa phiri la Sinai, Mose anatsogolera pa mwambo woika Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe. (Eks. 40:17; Lev. 9:1-5) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti akusangalala ndi ansembe atsopanowo? Pamene Aroni ndi Mose ankadalitsa anthu, Yehova anatumiza moto umene unapsereza nsembe zomwe zinatsala paguwa. (Lev. 9:23, 24) Kodi zimene zinachitika pa nthawi yoika ansembe atsopano zinasonyeza chiyani? Zinasonyeza kuti Yehova ankasangalala kwambiri ndi ansembe a m’banja la Aroni. Aisiraeli ataona kuti Yehova akusangalala ndi ansembewo anazindikira kuti ndi bwino kuchita zinthu mogwirizana nawo. Kodi nkhani imeneyi ikutikhudza bwanji? Ansembe a ku Isiraeli ankaimira ansembe ena abwino komanso ofunika kwambiri omwe ndi anthu 144,000 amene adzatumikira limodzi ndi Khristu kumwamba. (Aheb. 4:14; 8:3-5; 10:1) N’zosachita kufunsa kuti Yehova akutsogolera komanso kudalitsa gulu lake masiku ano. w19.11 23 ¶13; 24 ¶14, 16
Lachisanu, December 24
Tinagwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.—2 Ates. 3:8.
Ali ku Korinto, Mtumwi Paulo ankakhala ndi Akula ndi Purisikila ndipo “ankagwira ntchito pamodzi pakuti onse anali amisiri opanga mahema.” Koma mawu oti Paulo ankagwira ntchito “usiku ndi usana” sakutanthauza kuti ankagwira ntchito popanda kupuma. Iye ankapuma masiku ena monga pa Sabata. Pa tsikulo ankakhala ndi mwayi wolalikira Ayuda omwe sankagwiranso ntchito pa Sabata. (Mac. 13:14-16, 42-44; 16:13; 18:1-4) Paulo ankafunika kugwira ntchito zina koma ankagwirabe ntchito yopatulika “yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 15:16; 2 Akor. 11:23) Paulo ankalimbikitsa anthu ena kuti azichitanso zimenezi. Ndipo Akula ndi Purisika anali ‘antchito anzake mwa Khristu Yesu.’ (Aroma 12:11; 16:3) Paulo ankalimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti azikhala ndi “zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58; 2 Akor. 9:8) Yehova anauzira Paulo kulemba kuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”—2 Ates. 3:10. w19.12 5 ¶12-13
Loweruka, December 25
Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.—Sal. 127:3.
Yehova analenga anthu oyambirira m’njira yoti azifuna kubereka ana. Koma kodi ndi ndani amene ayenera kusankha ngati banja likufunika kubereka ana komanso nthawi yobereka anawo? M’zikhalidwe zina, anthu ambiri amaona kuti anthu amene akwatirana kumene ayenera kuyamba msanga kubereka ana. Anthu a pa banjawo akhoza kukakamizidwa ndi achibale kapena anthu ena kuti abereke msanga. M’bale wina wa ku Asia dzina lake Jethro anati: “Anthu ena mumpingo amene ali ndi ana amakakamiza mabanja ena kuti nawonso abereke.” M’bale winanso wa ku Asia dzina lake Jeffrey ananena kuti: “Anthu ena amauza mabanja amene alibe ana kuti adzasowa owasamalira akadzakalamba.” Koma ndi udindo wa banja lililonse kusankha kuti likhale ndi ana kapena ayi. (Agal. 6:5) N’zoona kuti achibale komanso anzawo a anthu amene akwatirana kumene angafune kuti banja latsopanolo lizisangalala. Koma onse ayenera kukumbukira kuti banjalo ndi limene liyenera kusankha kubereka ana kapena ayi.—1 Ates. 4:11. w19.12 22 ¶1-3
Lamlungu, December 26
Koma inu muzipemphera motere: “Atate wathu.”—Mat. 6:9.
Kodi zimakuvutani kuona Yehova ngati Atate wanu? Ena amadziona kuti ndi aang’ono komanso osafunika akadziyerekezera ndi Yehova. Iwo amakayikira zoti Mulungu Wamphamvuyonse amawawerengera. Koma Atate wathu wachikondi safuna kuti tizikhala ndi maganizo amenewa. Iye anatipatsa moyo ndipo amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Paulo ali ku Atene ananenanso mfundo imeneyi ndipo kenako ananena kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:24-29) Mulungu amafuna kuti tonse tizilankhula naye momasuka ngati mmene mwana amalankhulira ndi kholo lake lachikondi. Ena amavutika kuona kuti Yehova ndi Atate wawo chifukwa choti sanasonyezedwe chikondi ndi bambo awo enieni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zomwe mlongo wina ananena. Iye anati: “Bambo anga anali ankhanza kwambiri. Nditangoyamba kuphunzira Baibulo, zinkandivuta kuona Yehova ngati Atate wanga wakumwamba. Koma nditamudziwa bwino, maganizo amenewa anasintha.” Ngati inunso zimakuvutani, dziwani kuti mukhoza kuyamba kuona kuti Yehova ndi Atate wabwino kwambiri. w20.02 3 ¶4-5
Lolemba, December 27
Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.—Sal. 71:9.
Yesu anasonyeza kuti Yehova amayamikira zilizonse zimene tingachite pomutumikira tikamakula ngakhale zitaoneka zochepa kwambiri. (Sal 92:12-15; Luka 21:2-4) Choncho muziganizira kwambiri zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, mukhoza kuuza anthu za Yehova, kupempherera abale anu komanso kulimbikitsa anthu ena kuti akhalebe okhulupirika. Yehova amaona kuti ndinu wantchito mnzake ngati muli ndi mtima womumvera osati chifukwa chochita zinthu zambiri pomutumikira. (1 Akor. 3:5-9) Timayamikira kwambiri kutumikira Yehova Mulungu, yemwe amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali. Iye anatilenga kuti tizichita zimene amafuna ndipo tikamamulambira timakhala osangalala. (Chiv. 4:11) M’dzikoli, tikhoza kumaoneka ngati osanunkha kanthu koma Yehova sachita nafe manyazi. (Aheb. 11:16, 38) Mwina tingafooke chifukwa cha matenda, mavuto azachuma kapena ukalamba. Koma tizikumbukira kuti palibe chimene chingatilekanitse ndi chikondi cha Atate wathu wakumwamba.—Aroma 8:38, 39. w20.01 18 ¶16; 19 ¶18-19
Lachiwiri, December 28
Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.—Sal. 51:10.
Kukhala odzichepetsa komanso kukhutira ndi zimene tili nazo kungatithandize kupewa nsanje. Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino, nsanje singakule mumtima mwathu. Kudzichepetsa kumathandiza munthu kuti azidziona moyenera komanso azipewa kuganiza kuti ndi woyenera kukhala ndi zinthu zabwino kuposa aliyense. (Agal. 6:3, 4) Munthu wokhutira ndi zimene ali nazo sadziyerekezera ndi anthu ena. (1 Tim. 6:7, 8) Munthu wodzichepetsa komanso wokhutira ndi zimene ali nazo amasangalala akaona kuti munthu wina walandira zinthu zabwino. Tiyenera kuthandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kuti tipewe nsanje n’kumakhala odzichepetsa ndiponso okhutira ndi zimene tili nazo. (Agal. 5:16; Afil. 2:3, 4) Mzimu woyera wa Yehova ungatithandize kudzifufuza kuti tidziwe zonse zimene zili m’maganizo komanso mumtima mwathu. Mulungu angatithandize kuchotsa maganizo oipa n’kukhala ndi maganizo abwino.—Sal. 26:2. w20.02 15 ¶8-9
Lachitatu, December 29
Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.
Pamene munkadzipereka, munalumbira kwa Yehova ndipo iye amafuna kuti mukwaniritse zimene munalonjeza. Muyenera kugwirizana kwambiri ndi anthu mumpingo. Mukamasonkhana nawo nthawi zonse, ubwenzi wanu umakhala wolimba. Muyenera kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Sal. 1:1, 2) Mukamaliza kuwerenga, muzipeza nthawi yoganizira mozama zimene mwawerengazo. Mukatero, mfundo zake zikhoza kukufikani pamtima. Muyeneranso ‘kupemphera kosalekeza.’ (Mat. 26:41) Munthu akamapemphera kuchokera pansi pa mtima, ubwenzi wake ndi Yehova umalimba kwambiri. Komanso “pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.” (Mat. 6:33) Mungachite zimenezi ngati mumaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri pa moyo wanu. Mukamalalikira nthawi zonse, chikhulupiriro chanu chimalimba. Mavuto amene mungakumane nawo m’dzikoli “ndi akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Koma mukadzipereka ndi kubatizidwa mudzapeza madalitso panopa komanso “moyo weniweniwo” m’tsogolo. Choncho kudzipereka ndiponso kubatizidwa ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu kuposa chilichonse.—1 Tim. 6:19. w20.03 13 ¶19-21
Lachinayi, December 30
Nthawi yotsalayi yafupika.—1 Akor. 7:29.
Ngati munthu amene tikuphunzira naye sakusintha moyo wake, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndipitirize kuphunzira naye kapena ndimusiye?’ Musanasankhe zochita pa nkhaniyi ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi munthuyu akuyesetsa kuchita zimene angathe? Kodi wayamba “kusunga,” kapena kuti kutsatira, zimene akuphunzira?’ (Mat. 28:20) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena ali ngati Aisiraeli a m’nthawi ya Ezekieli. Yehova anauza Ezekieli kuti: “Kwa iwo uli ngati munthu woimba nyimbo zachikondi. Uli ngati munthu wa mawu anthetemya komanso wodziwa kuimba choimbira cha zingwe. Iwo adzamva ndithu mawu ako, koma palibe amene adzawatsatire.” (Ezek. 33:32) N’zoona kuti zimakhala zovuta kuuza munthu kuti tisiya kuphunzira naye. Koma tizikumbukira kuti “nthawi yotsalayi yafupika.” M’malo mokakamira kuphunzira ndi munthu amene sakusintha, ndi bwino kufufuza anthu ena amene akusonyeza kuti ‘ali ndi maganizo abwino owathandiza kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48. w20.01 6 ¶17; 7 ¶20
Lachisanu, December 31
Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.—Mat. 6:10.
Matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu saphunzitsa mfundo ya m’Malemba yakuti anthu omvera Mulungu adzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. (2 Akor. 4:3, 4) Masiku ano, zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti anthu onse abwino akamwalira amapita kumwamba. Koma Ophunzira Baibulo ochepa, amene ankafalitsa Nsanja ya Olonda kuyambira mu 1879, sankaphunzitsa zimenezi. Iwo ankakhulupirira kuti Mulungu adzabwezeretsa Paradaiso padzikoli ndipo anthu omvera Mulungu ambirimbiri adzakhala padzikoli osati kumwamba. Koma zinawatengera nthawi kuti azindikire kuti anthu omverawo ndi ndani. Ophunzira Baibulo anazindikiranso kuti Malemba amaphunzitsa kuti anthu ena ‘adzagulidwa kuchokera padziko lapansi’ kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. (Chiv. 14:3) Anthu amenewa ndi Akhristu okwana 144,000 omwe amatumikira Mulungu mokhulupirika pa nthawi imene ali padzikoli. w19.09 27 ¶4-5