Makhalidwe Olakwika
Kodi Akhristu ayenera kupewa makhalidwe olakwika ati?
Mkwiyo
Sl 37:8, 9; Miy 29:22; Akl 3:8
Onaninso Miy 14:17; 15:18
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 37:18, 19, 23, 24, 31-35—Azibale ake a Yosefe anamuukira, kumugulitsa ngati kapolo komanso ananamiza Yakobo kuti mwana wake wokondedwa Yosefe wamwalira
Ge 49:5-7—Simiyoni ndi Levi anaweruzidwa chifukwa chakuti atakwiya, anachita zinthu zoipa kwambiri
1Sa 20:30-34—Sauli atakwiya ananyoza mwana wake Yonatani ndipo ankafuna kumupha
1Sa 25:14-17—Nabala analalatira anthu amene anatumizidwa ndi Davide, ndipo zimenezi zinaika pangozi moyo wa anthu onse am’banja lake
Kukonda mikangano
Mzimu wamantha
Nkhanza
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 42:21-24—Azichimwene a Yosefe anadzimvera chisoni chifukwa cha nkhanza zomwe anachitira Yosefe
Mko 3:1-6—Yesu anakhumudwa kwambiri chifukwa cha nkhanza zimene Afarisi ankachitira anthu
Kupanda ulemu
Onaninso “Kupanda Ulemu”
Kudzikudza
Ga 5:26; Afi 2:3
Onaninso Miy 3:7; 26:12; Aro 12:16
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Sa 15:1-6—Abisalomu anali wodzikuza ndipo ankakopa mitima ya anthu n’cholinga choti asamamvere Mfumu Davide bambo ake
Da 4:29-32—Mfumu Nebukadinezara anali wonyada ndipo mapeto ake Yehova anamulanga
Nsanje; kusirira mwansanje
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 26:12-15—Yehova anadalitsa Isaki chifukwa chogwira ntchito mwakhama koma Afilisiti anayamba kumuchitira nsanje
1Mf 21:1-19—Ahabu Mfumu yoipa anasirira munda wa mpesa wa Naboti ndipo mapeto ake Naboti anaimbidwa mlandu wabodza n’kuphedwa
Kuopa anthu
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Nu 13:25-33—Pa Aisiraeli 12 omwe anatumidwa kukazonda dziko la Kanani, 10 mwa iwo anachita mantha ndipo anachititsa kuti anthu ena onse achitenso mantha
Mt 26:69-75—Mtumwi Petulo anakana Yesu katatu chifukwa choopa anthu
Dyera
Onani “Dyera”
Chidani
Onaninso Nu 35:19-21; Mt 5:43, 44
Chinyengo
Onani “Chinyengo”
Nsanje
Onani “Nsanje”
Ulesi
Miy 6:6-11; Mla 10:18; Aro 12:11
Onaninso Miy 10:26; 19:15; 26:13
Kukonda ndalama; zinthu zakuthupi
Onaninso 1Yo 2:15, 16
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yob 31:24-28—Ngakhale kuti anali munthu wolemera, Yobu anapewa msampha wokonda chuma
Mko 10:17-27—Mwamuna wina wachuma ankakonda kwambiri chuma chake moti anakana kutsatira Yesu
Kupsa mtima kwambiri
Onaninso Yak 3:14
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ob 10-14—Mulungu analanga Aedomu chifukwa choti anapsera mtima kwambiri abale awo Aisiraeli
Kudzikuza
Onani “Kudzikuza”
Kunyada; kudzikuza
Onani “Kunyada”
Wokonda mikangano
Kupanduka
Onaninso De 21:18-21; Sl 78:7, 8; Tit 1:10
Kudziona wolungama
Mla 7:16; Mt 7:1-5; Aro 14:4, 10-13
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 12:1-7—Yesu anaulula kuti Afarisi anali ndi mtima wodziona kuti ndi olungama
Lu 18:9-14—Yesu ananena fanizo losonyeza kuti Mulungu sasangalala ndi anthu odziona kuti ndi olungama
Kuuma mtima
Onaninso Yer 7:23-27; Zek 7:11, 12
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mb 36:11-17—Zedekiya anali mfumu youma mtima ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu amtundu wake alangidwe ndi Mulungu
Mac 19:8, 9—Mtumwi Paulo anasiya kulalikira kwa anthu omwe anaumitsa mitima yawo kuti asamvetsere uthenga wa Ufumu
Kupanda nzeru
Onaninso 1Pe 2:15
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 8:10-20—Aisiraeli anakana kumvera mneneri Samueli atawauza kuti si nzeru kudzisankhira mfumu
1Sa 25:2-13, 34—Nabala akanaphetsa anthu a m’banja lake onse chifukwa chokana kumvetsera pempho la Davide
Kukayikira ena kapena kuwaganizira zolakwika
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 18:6-9; 20:30-34—Mfumu Sauli ankaganiza kuti Davide ndi wosakhulupirika ndipo ankafuna kuti Yonatani azimutsutsa