January
Loweruka, January 1
Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.—2 Tim. 3:15.
Timoteyo anali ndi chikhulupiriro chifukwa choti anakhutira ndi mfundo za m’Baibulo zimene zinamuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Nanunso muyenera kumaphunzira Baibulo n’kufika pokhutira kuti zimene mwaphunzira zokhudza Yehova ndi zoona. Kuti tifike pokhutira ndi zimene timaphunzira, choyamba tiyenera kutsimikizira kuti mfundo zoyambirira za choonadi zitatu izi ndi zoona. Mfundo yoyamba ndi yakuti Yehova Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. (Eks. 3:14, 15; Aheb. 3:4; Chiv. 4:11) Yachiwiri ndi yakuti Baibulo ndi uthenga wochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu. (2 Tim. 3:16, 17) Ndipo yachitatu ndi yakuti Yehova ali ndi gulu lake limene limamulambira motsogoleredwa ndi Khristu ndipo gulu limeneli ndi la Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12; Yoh. 14:6; Mac. 15:14) Kuchita zimenezi sikuchita kufuna kuti munthu adziwe chilichonse chokhudza Baibulo. Cholinga chanu chizikhala choti muzigwiritsa ntchito mphamvu zanu za kuganiza kuti musamakayikire zoti zimene mumakhulupirira ndi zoona.—Aroma 12:1. w20.07 10 ¶8-9
Lamlungu, January 2
Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze miyezi isanu.—Chiv. 9:5.
Ulosiwu umanena za dzombe lomwe lili ndi nkhope za anthu ndipo pamitu pawo pali “zisoti zagolide zooneka ngati zachifumu.” (Chiv. 9:7) Ndipo likuzunza adani a Mulungu kapena kuti anthu “amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.” Likuchita zimenezi kwa miyezi 5 yomwe ikuimira nthawi imene dzombe lenileni limakhala moyo. (Chiv. 9:4) Apa zikuonekeratu kuti ulosiwu ukunena za atumiki a Yehova odzozedwa. Iwo amalalikira molimba mtima uthenga wakuti Mulungu adzaweruza dziko loipali ndipo izi zimachititsa kuti anthu m’dzikoli asamasangalale nawo. Kodi pamenepa tikutanthauza kuti dzombe lofotokozedwa pa Yoweli 2:7-9 ndi losiyana ndi limene likupezeka m’buku la Chivumbulutso? Inde. M’Baibulo chinthu chimodzi chikhoza kuimira zinthu zosiyana. Mwachitsanzo, pa Chivumbulutso 5:5 Yesu amatchulidwa kuti “Mkango wa fuko la Yuda” pomwe pa 1 Petulo 5:8 pamanena kuti Mdyerekezi ndi “mkango wobangula.” w20.04 3 ¶8; 5 ¶10
Lolemba, January 3
Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.—Miy. 15:3.
Hagara, yemwe anali wantchito wa Sarai, anachita zinthu mopusa ataloledwa kuti akhale mkazi wa Abulamu. Iye atakhala woyembekezera anayamba kunyoza Sarai chifukwa choti analibe mwana. Zinthu zinafika poipa kwambiri moti Sarai anayamba kumuzunza ndipo anathawa. (Gen. 16:4-6) Popeza si ife angwiro, tikhoza kuganiza kuti Hagara anali wamwano ndipo m’pake kuti ankamuzunza. Koma umu si mmene Yehova ankamuonera. Iye anatumiza mngelo amene anathandiza Hagara kuti asinthe maganizo ake ndipo kenako anamudalitsa. Hagara anazindikira kuti Yehova ankaona zonse zimene zinkamuchitikira. Iye anafika ponena kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.” Ananenanso kuti Mulungu amamuona iyeyo. (Gen. 16:7-13) Kodi ndi zinthu ziti zokhudza Hagara zimene Yehova ankadziwa? Iye ankadziwa mmene anakulira komanso zimene anakumana nazo pa moyo wake. w20.04 16 ¶8-9
Lachiwiri, January 4
Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.—2 Tim. 4:7.
Mtumwi Paulo ananena kuti Akhristu oona onse ali pa mpikisano. (Aheb. 12:1) Ndipo tonsefe, kaya ndife achinyamata kapena achikulire, amphamvu kapena ofooka, tiyenera kuthamanga mopirira mpaka pa mapeto ngati tikufuna kudzapeza mphoto imene Yehova adzatipatse. (Mat. 24:13) Paulo anali ndi ufulu wolankhula pa nkhaniyi chifukwa anali ‘atathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.’ (2 Tim. 4:7, 8) Koma kodi mpikisano umene Paulo anatchulawo ndi wotani? Nthawi zina, Paulo ankagwiritsa ntchito zinthu zimene zinkachitika pa masewera a ku Girisi pofuna kuphunzitsa mfundo zina zofunika. (1 Akor. 9:25-27; 2 Tim. 2:5) Maulendo angapo, iye anayerekezera moyo wa Mkhristu ndi mpikisano wothamanga. (1 Akor. 9:24; Agal. 2:2; Afil. 2:16) Munthu amayamba nawo ‘mpikisanowu’ akadzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. (1 Pet. 3:21) Ndipo amamaliza mpikisanowu Yehova akamupatsa mphoto ya moyo wosatha.—Mat. 25:31-34, 46; 2 Tim. 4:8. w20.04 26 ¶1-3
Lachitatu, January 5
Nyamulani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.—Aef. 6:13.
“Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.” (2 Ates. 3:3) Kodi Yehova amatiteteza bwanji? Yehova watipatsa zida zankhondo zomwe zingatiteteze Satana akamatiukira. (Aef. 6:13-17) Zidazi ndi zamphamvu komanso zodalirika. Koma kuti titetezeke, nthawi zonse tiyenera kuvala komanso kugwiritsa ntchito chida chilichonse. Mwachitsanzo lamba wachoonadi amaimira choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. N’chifukwa chiyani tiyenera kuvala lamba ameneyu? Chifukwa Satana ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Iye wakhala akunama kwa zaka zambiri ndipo wasocheretsa “dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chiv. 12:9) Koma choonadi cha m’Baibulo chimatiteteza kuti tisanamizidwe. Kodi timavala bwanji lamba wophiphiritsirayu? Timavala lambayu pophunzira choonadi chonena za Yehova, kumulambira “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi” komanso poyesetsa kuchita zinthu moona mtima.—Yoh. 4:24; Aef. 4:25; Aheb. 13:18. w21.03 26-27 ¶3-5
Lachinayi, January 6
Iyo idzalowanso m’Dziko Lokongola.—Dan. 11:41.
Chimene chinkapangitsa dzikoli kukhala lapadera n’chakuti ndi komwe anthu ankalambirako Yehova. Koma kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., “dziko” lokongolali si dziko linalake lapadera. Tikutero chifukwa masiku ano anthu a Mulungu akupezeka kulikonse padziko lapansi. Choncho masiku ano, “dziko lokongola” likuimira zimene anthu a Yehova amachita monga kusonkhana komanso kulalikira. M’masiku otsiriza, mfumu ya kumpoto yakhala ikulowa mobwerezabwereza mu “dziko lokongola.” Mwachitsanzo, pamene dziko la Germany linali mfumu ya kumpoto, makamaka pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, mfumuyi inalowa mu “dziko lokongola” pozunza ndi kupha anthu a Mulungu. Komanso nkhondoyi itatha, mfumu ya kumpoto imene pa nthawiyo inali boma la Soviet Union, inalowanso mu “dziko lokongola” pozunza anthu a Mulungu komanso kuwathamangitsira m’mayiko ena. w20.05 13 ¶7-8
Lachisanu, January 7
Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa, pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.—Sal. 25:14.
Taganizirani zitsanzo za anthu amene anakhalako Chikhristu chisanayambe omwe anali mabwenzi a Mulungu. Abulahamu anali munthu wachikhulupiriro cholimba. Patadutsa zaka zoposa 1,000 Abulahamu atamwalira, Yehova anamutchula kuti “bwenzi langa.” (Yes. 41:8) Zimenezi zikutanthauza kuti ngakhale anthu amwalire, Yehova amawaonabe kuti ndi mabwenzi ake a pamtima. Tingati kwa Yehova, Abulahamu adakali wamoyo. (Luka 20:37, 38) Chitsanzo china ndi Yobu. Pamene angelo anasonkhana kumwamba, Yehova analankhula motsimikiza zokhudza kukhulupirika kwa Yobu. Iye anamutchula kuti anali “munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.” (Yobu 1:6-8) Nayenso Danieli anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka pafupifupi 80 ali m’dziko la anthu amene sankalambira Yehova. Ndiye kodi Yehova ankamuona bwanji? Katatu konse angelo anamutsimikizira kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri” ndi Mulungu. (Dan. 9:23; 10:11, 19) N’zoonekeratu kuti Yehova amachita kulakalaka kuti adzaukitse mabwenzi ake a pamtima omwe anamwalira.—Yobu 14:15. w20.05 26-27 ¶3-4
Loweruka, January 8
Ndiphunzitseni malamulo anu.—Sal. 119:68.
Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, tingawathandize kuti adziwe malamulo a Mulungu n’kumawaona kuti ndi abwino. Koma kodi kungodziwa malamulowo kungawathandize kuti azimumvera chifukwa choti amamukonda? Tisaiwale kuti Hava ankadziwa lamulo la Mulungu, koma iye ndi Adamu sankakonda Mulungu yemwe anawapatsa lamulolo. (Gen. 3:1-6) Choncho tiyenera kuchita zambiri osati kungophunzitsa anthu zimene Mulungu amafuna. Nthawi zonse malamulo a Yehova ndi abwino. (Sal. 119:97, 111, 112) Koma anthu amene timaphunzira nawo Baibulo sangawaone choncho ngati sitinawathandize kudziwa kuti Yehova anapereka malamulowo chifukwa choti amatikonda. Choncho tingachite bwino kuwafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti atumiki ake azichita zinazake kapena asamachite zinazake? Kodi zimenezi zikutiuza chiyani za iyeyo?” Tikamathandiza amene timaphunzira nawo kuganizira za Yehova ndi kuyamba kukonda kwambiri dzina lake, tingawafikedi pamtima. Iwo angayambe kukonda malamulo ake komanso Wopereka Malamuloyo. Ndipo adzakhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso zidzawathandiza kuti adzapirire mayesero ovuta m’tsogolo.—1 Akor. 3:12-15. w20.06 10 ¶10-11
Lamlungu, January 9
Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.—Yak. 1:19.
Timafunika kukhala oleza mtima chifukwa pamatenga nthawi kuti munthu abwerere kwa Yehova. Anthu ena amene anasiya kusonkhana m’mbuyomu anafotokoza kuti anayambiranso kusonkhana akulu ndi Akhristu ena atawayendera mobwerezabwereza. Mlongo wina wa ku Asia, dzina lake Nancy ananena kuti: “Mnzanga wina wamumpingo anandithandiza kwambiri. Ankandikonda kwambiri ngati mkulu wake. Anandikumbutsa zinthu zabwino zimene tinachitirapo limodzi. Ankandimvetsera moleza mtima ndikamafotokoza mmene ndikumvera ndipo sankazengereza kundipatsa malangizo. Analidi mnzanga weniweni ndipo anali wokonzeka kundithandiza nthawi iliyonse.” Kuchitira ena chifundo kuli ngati mankhwala othandiza munthu amene wakhumudwa. Ena anasiya kusonkhana chifukwa choti anakhumudwitsidwa ndi munthu wina mumpingo. Ngakhale kuti panadutsa nthawi yaitali, zimawapwetekabe ndipo zimawavuta kuti abwererenso kwa Yehova. Enanso amaona kuti sanachitiridwe zachilungamo. Ndiye amafuna munthu amene angawamvetsere komanso kuwamvetsa. w20.06 26 ¶10-11
Lolemba, January 10
Mwagonjetsa woipayo.—1 Yoh. 2:14.
Mukamayesetsa kupewa mayesero, zimakhala zosavuta kuti muzichita zoyenera. Muzikumbukiranso kuti Satana ndi amene amachititsa kuti anthu a m’dzikoli azikhala ndi maganizo olakwika okhudza kugonana. Choncho mukamayesetsa kukana mayesero, mumakhala ‘mukugonjetsa woipayo.’ Timadziwa kuti Yehova ndi amene angatiuze ngati khalidwe linalake lili tchimo kapena ayi. Ndipo timayesetsa kuti tisamachite machimo. Koma tikachimwa, timapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti atikhululukire. (1 Yoh. 1:9) Ndipo tikachita tchimo lalikulu, timapempha akulu kuti atithandize. Yehova anapatsa akuluwa udindo woti azitisamalira. (Yak. 5:14-16) Komabe ngati tinakonza zinthu, sitiyenera kumadziimba mlandu chifukwa cha machimo omwe tinachita kalekale. Tikutero chifukwa Atate wathu wachikondi anapereka Mwana wake nsembe kuti azitikhululukira machimo athu. Choncho tisamakaikire zimene amatiuza kuti adzatikhululukira ngati talapadi kuchokera mumtima. Apatu tinganene kuti palibe chomwe chingatilepheretse kumatumikira Yehova ndi chikumbumtima choyera.—1 Yoh. 2:1, 2, 12; 3:19, 20. w20.07 22-23 ¶9-10
Lachiwiri, January 11
Inu ndinu kasupe wa moyo.—Sal. 36:9.
Pa nthawi ina, Yehova anali yekhayekha koma zimenezi sizinkachititsa kuti asamasangalale. Tikutero chifukwa iye safunikira kukhala ndi winawake kuti azisangalala. Komabe Mulungu ankafuna kuti enanso akhale ndi moyo n’kumasangalala. Choncho chifukwa cha chikondi chake, iye anayamba kugwira ntchito yolenga. (1 Yoh. 4:19) Choyamba, Yehova analenga Mwana wake, Yesu. Ndiyeno limodzi ndi Mwana wakeyo, analenga “zinthu zina zonse” kuphatikizapo angelo. (Akol. 1:16) Yesu ankasangalala kugwira ntchito ndi Atate wake. (Miy. 8:30) Angelo nawonso anasangalala. Iwo analipo ndipo anaona pamene Yehova ndi mmisiri wake Yesu, ankalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi angelowo anasonyeza bwanji kuti anasangalala? Iwo “anayamba kufuula ndi chisangalalo” pamene dziko lapansi linalengedwa ndipo n’zosakayikitsa kuti anapitirizabe kusangalala ndi zinthu zonse zimene Yehova analenga, kuphatikizapo anthu. (Yobu 38:7; Miy. 8:31) Zimene Yehova analengazi zimasonyeza kuti iye ndi wachikondi komanso wanzeru.—Sal. 104:24; Aroma 1:20. w20.08 14 ¶1-2
Lachitatu, January 12
Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.—Mat. 24:9.
Yehova anatilenga kuti tizikonda anthu ena komanso kuti anthu enawo azitikonda. Choncho munthu wina akamadana nafe, timakhumudwa ndipo mwinanso timachita mantha. M’bale wina analemba kuti: “Asilikali atandimenya, kundinyoza komanso kundiopseza chifukwa choti ndine wa Mboni za Yehova, ndinachita mantha ndiponso ndinachita manyazi kwambiri.” Anthu ena akamadana nafe, zimatiwawa komabe zimenezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa Yesu ananeneratu kuti ena adzadana nafe. N’chifukwa chiyani dzikoli limadana ndi otsatira a Yesu? Chifukwa mofanana ndi Yesu, ‘sitili mbali ya dzikoli.’ (Yoh. 15:17-19) Choncho ngakhale kuti timalemekeza maboma a anthu, sitimawalambira kapena kulemekeza zizindikiro zoimira mabomawo. Ife timalambira Yehova yekha basi. Timaona kuti Mulungu ndi amene ali woyenera kulamulira anthu koma Satana ndi “mbewu” yake amatsutsa kwambiri zimenezi. (Gen. 3:1-5, 15) Timalalikira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetse mavuto onse a anthu komanso kuti Ufumuwu posachedwapa, uwononga onse otsutsa. (Dan. 2:44; Chiv. 19:19-21) Umenewutu ndi uthenga wabwino kwa anthu ofatsa koma kwa oipa, ndi wosasangalatsa. w21.03 20 ¶1-2
Lachinayi, January 13
Tikudziwa kuti tinachokera kwa Mulungu.—1 Yoh. 5:19.
Yehova amasonyezanso kuti alongo ndi amtengo wapatali powapatsa ntchito yofunika kwambiri mumpingo. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za akazi amene anakondweretsa Mulungu. Akazi amenewa anali zitsanzo zabwino pankhani yosonyeza chikhulupiriro, nzeru, kudzipereka, kulimba mtima, kupatsa ndi ntchito zina zabwino. (Luka 8:2, 3; Mac. 16:14, 15; Aroma 16:3, 6; Afil. 4:3; Aheb. 11:11, 31, 35) Timasangalalanso kuti tili ndi achikulire ambiri m’mipingo yathu. Ngakhale kuti achikulirewa amavutika ndi matenda amene amabwera chifukwa cha ukalamba, iwo amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe mu utumiki ndipo amagwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti alimbikitse komanso kuphunzitsa ena. Anthu amenewa akumana ndi zambiri pa moyo wawo ndipo tingapindule kwambiri ndi zitsanzo zawo. Kunena zoona anthuwa ndi ofunika kwambiri kwa Yehova komanso kwa ife. (Miy. 16:31) Tilinso ndi achinyamata m’mipingo yathu. Iwo amakumana ndi mavuto ambiri chifukwa akukulira m’dziko limene wolamulira wake ndi Satana Mdyerekezi, yemwe amasokoneza maganizo a anthu. Komabe timasangalala tikaona achinyamatawa akuyankha pamisonkhano, kulalikira komanso kufotokoza molimba mtima zimene amakhulupirira. Achinyamatanu, dziwani kuti ndinu ofunika kwambiri mumpingo wa Yehova.—Sal. 8:2. w20.08 21-22 ¶9-11
Lachisanu, January 14
Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.—Mat. 10:16.
Tikangoyamba kulalikira komanso kudziwika monga wa Mboni za Yehova, tingakumane ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, achibale athu angamatitsutse, anzathu angamatinyoze komanso ena angakane kumvetsera uthenga wathu. N’chiyani chingakuthandizeni kukhala olimba mtima? Choyamba, musamakayikire kuti Yesu akupitirizabe kutsogolera ntchito yolalikira. (Yoh. 16:33; Chiv. 14:14-16) Chachiwiri, muzikhulupirira zimene Yehova analonjeza zoti adzakusamalirani. (Mat. 6:32-34) Chikhulupiriro chanu chikamalimba, m’pamenenso mumayamba kukhala olimba mtima kwambiri. Inuyo munasonyeza kuti muli ndi chikhulupiriro cholimba pamene munauza anzanu komanso achibale anu kuti mwayamba kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. Sitikukayikira kuti mwasintha zinthu zambiri pa moyo wanu kuti muzitsatira mfundo zolungama za Yehova. Kuchita zimenezi kumafunanso chikhulupiriro komanso kulimba mtima. Mukamapitiriza kuchita zinthu molimba mtima, musamakayikire kuti ‘Yehova Mulungu adzakhala nanu kulikonse kumene mungapite’.—Yoswa 1:7-9. w20.09 5 ¶11-12
Loweruka, January 15
Yehova anam’patsa mpumulo.—2 Mbiri 14:6.
Mfumu Asa ndi chitsanzo chabwino chifukwa anachita zinthu mwanzeru podalira Yehova ndi mtima wake wonse. Iye anatumikira Yehova pa nthawi yovuta komanso pa nthawi imene zinthu zinali bwino. Kuyambira ali wamng’ono, “Asa anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 15:14) Asa anasonyeza kuti ankatumikira Yehova ndi mtima wonse pamene anathetsa kulambira konyenga ku Yuda. Baibulo limanena kuti “iye anachotsa maguwa ansembe achilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:3, 5) Anachotsanso agogo ake aakazi a Maaka pa udindo wawo monga amayi a mfumu. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa chakuti agogo akewo ankalimbikitsa anthu kulambira fano. (1 Maf. 15:11-13) Asa anachita zinthu zinanso zambiri. Mwachitsanzo, anathandiza anthu a ku Yuda kuti ayambirenso kutumikira Yehova. Yehova anadalitsa Asa komanso anthu a ku Yuda powapatsa mtendere. Kwa zaka 10 mu ulamuliro wake, “m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse.”—2 Mbiri 14:1, 4, 6. w20.09 14 ¶2-3
Lamlungu, January 16
Timoteyo, sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako.—1 Tim. 6:20.
Nthawi zambiri timasungitsa ena zinthu zathu zamtengo wapatali. Mwachitsanzo, timasungitsa ndalama zathu kubanki. Tikatero, timakhulupirira kuti ndalamazo sizingasowe kapena kubedwa. Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti anapatsidwa chinthu chinachake chamtengo wapatali, chomwe ndi choonadi chokhudza cholinga chimene Mulungu ali nacho kwa anthu. Timoteyo anapatsidwanso mwayi ‘wolalikira mawu’ komanso ‘wogwira ntchito ya mlaliki.’ (2 Tim. 4:2, 5) Choncho Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti aziteteza zinthu zimene anapatsidwa. Mofanana ndi Timoteyo, nafenso tapatsidwa zinthu zamtengo wapatali. Yehova anatipatsa choonadi chamtengo wapatali chomwe chimapezeka m’Mawu ake, Baibulo. Choonadichi ndi chamtengo wapatali chifukwa chimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova. Komanso chimafotokoza zimene tingachite kuti tikhale osangalala. Tikaphunzira choonadi n’kumayesetsa kutsatira mfundo zake, timamasuka ku ukapolo wa ziphunzitso zabodza komanso makhalidwe oipa.—1 Akor. 6:9-11. w20.09 26 ¶1-3
Lolemba, January 17
Inuyo mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani.—1 Ates. 1:5.
Wophunzira wanu aziona kuti mumakonda komanso kukhulupirira zimene Baibulo limaphunzitsa. Zimenezi zingamuthandize kuti nayenso azikonda kwambiri zimene akuphunzira. Mwinanso mungamufotokozere mmene mfundo za m’Baibulo zakuthandizirani pa moyo wanu. Mukamachita zimenezi, wophunzirayo angayambe kuzindikira kuti m’Baibulo muli malangizo abwino amene angamuthandize. Tikamaphunzira Baibulo, tingafotokozere wophunzira za abale ndi alongo amene anakumananso ndi mavuto ofanana ndi ake ndiponso zimene anachita kuti athane nawo. Tikhozanso kupita kuphunzirolo ndi m’bale kapena mlongo ngati ameneyu n’cholinga choti akalimbikitse wophunzirayo. Tizithandiza wophunzirayo kuona kuti ndi nzeru kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Ngati wophunzirayo ali pabanja, kodi mwamuna kapena mkazi wake amaphunzira nawo? Ngati si choncho, mungamupemphe kuti azikhala nawo paphunzirolo. Muzilimbikitsa wophunzirayo kuti aziuza achibale komanso anzake zimene akuphunzira.—Yoh. 1:40-45. w20.10 16 ¶7-9
Lachiwiri, January 18
Ndi kuwakhomereza mwa ana ako.—Deut. 6:7.
Yosefe ndi Mariya anathandiza Yesu kuti akule ndi makhalidwe abwino amene Mulungu amasangalala nawo chifukwa ankatsatira malangizo amene Yehova anapereka kwa makolo. (Deuteronomo. 6:6, 7) Makolo a Yesu ankakonda kwambiri Yehova ndipo cholinga chawo chachikulu chinali chothandiza ana awo kuti azikondanso Yehova. Yosefe ndi Mariya anasankha kuti nthawi zonse azilambira Mulungu limodzi ndi ana awo. N’chifukwa chake mlungu uliwonse ankakasonkhana ku sunagoge ku Nazareti komanso chaka chilichonse ankapita kumwambo wa Pasika ku Yerusalemu. (Luka 2:41; 4:16) Pa maulendo opita ku Yerusalemuwa iwo ankapezerapo mwayi wophunzitsa Yesu ndi abale ake zinthu zimene zinachitikira anthu a Yehova m’mbuyomu. Komanso mwina ankaima kuti aone malo ena amene amatchulidwa m’Malemba. Pamene banja lawo linkakula sizinali zophweka kuti Yosefe ndi Mariya apitirize kuchita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse. Koma Mulungu anawadalitsa kwambiri chifukwa chopitiriza kuchita zimenezi. Banjali linapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova chifukwa chakuti linkaika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba. w20.10 28 ¶8-9
Lachitatu, January 19
Ezara anakonza mtima wake kuti aphunzire chilamulo cha Yehova . . . ndiponso kuti aphunzitse.—Ezara 7:10.
Ngati wina wakupemphani kuti mupite naye kuphunziro lake, mungachite bwino kukonzekera phunzirolo. Mpainiya wina wapadera dzina lake Daniel, anati: “Ndimasangalala ngati munthu amene ndapita naye kuphunziro wakonzekera bwino chifukwa ndi pamene amatha kufotokoza mfundo zothandiza.” Wophunzira amatha kuzindikira kuti nonse mwakonzekera bwino ndipo zimenezi zimamupatsa chitsanzo chabwino. Ngati simungakwanitse kukonzekera phunziro lonse, mungachite bwino kupeza nthawi kuti muone mfundo zazikulu m’phunzirolo. Pemphero ndi lofunika kwambiri paphunziro la Baibulo. Choncho muyenera kuganizira pasadakhale zimene munganene ngati mutapemphedwa kuti mupemphere. Zimenezi zingathandize kuti mutchule mfundo zofunika m’pempherolo. (Sal. 141:2) Hanae, yemwe amakhala ku Japan, amakumbukira mapemphero a mlongo wina amene ankabwera ndi mphunzitsi wake. Iye anati: “Ndinkaona kuti mlongoyo anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo ndinkafunitsitsa kukhala ngati iyeyo. Ndinkaonanso kuti amandikonda akamatchula dzina langa m’mapempherowo.” w21.03 9-10 ¶7-8
Lachinayi, January 20
Limba mtima! . . . ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.—Mac. 23:11.
Yesu anatsimikizira mtumwi Paulo kuti akafika ku Roma. Komabe Ayuda ena ku Yerusalemu anakonza chiwembu choti aphe Paulo. Mkulu wa asilikali a Chiroma dzina lake Kalaudiyo Lusiya atamva za chiwembu chimenechi anapulumutsa Paulo. Mwamsanga, Kalaudiyo analamula gulu la asilikali kuti ateteze Paulo ndi kum’tenga kupita naye ku Kaisareya. Kumeneko, Bwanamkubwa Felike analamula kuti Paulo “amusunge m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anira.” Ayuda amene ankafuna kupha Paulo aja sakanatha kufikako. (Mac. 23:12-35) Koma Felike analowedwa m’malo ndi Fesito amene anakhala bwanamkubwa watsopano. Iye “pofuna kuti Ayudawo amukonde,” anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?” Paulo ankadziwa kuti akapita ku Yerusalemu akhoza kukaphedwa. Iye anati: “Ndikupempha kuti ndikaonekere kwa Kaisara!” Fesito anauza Paulo kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekera kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Posakhalitsa Paulo anafika ku Roma komwe Ayuda amene ankafuna kumupha aja sakanatha kumupeza.—Mac. 25:6-12. w20.11 13 ¶4; 14 ¶8-10
Lachisanu, January 21
Mitima yathu ingatitsutse.—1 Yoh. 3:20.
Nthawi zina tonsefe timadziimba mlandu. Mwachitsanzo, ena amadziimba mlandu chifukwa cha zinthu zimene ankachita asanaphunzire choonadi. Enanso amadziimba mlandu chifukwa cha zolakwa zimene anachita atabatizidwa. (Aroma 3:23) N’zoona kuti timafuna kuchita zabwino, koma “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2; Aroma 7:21-23) Ngakhale kuti kudziimba mlandu sikosangalatsa, koma kumatithandiza m’njira zina. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa kudziimba mlandu n’kumene kungatithandize kuti tisinthe n’kutsimikiza mtima kuti tisadzabwerezenso zimene tinalakwitsazo. (Aheb. 12:12, 13) Komabe n’zotheka kumadziimba kwambiri mlandu. Zimenezi zikutanthauza kupitirizabe kudziimba mlandu ngakhale zitakhala kuti munthuyo analapa ndiponso Yehova anamukhululukira. Kudziimba mlandu kotereku kungakhale koopsa. (Sal. 31:10; 38:3, 4) Choncho tiyenera kusamala kuti tisamadziimbe mlandu mopitirira muyezo. Tikutero chifukwa Satana angasangalale kwambiri ngati titasiya kutumikira Yehova ngakhale kuti Yehovayo amatikondabe komanso anatikhululukira.—Yerekezerani ndi 2 Akor. 2:5-7, 11. w20.11 27 ¶12-13
Loweruka, January 22
Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.—Sal. 73:13.
Mlevi wina amene analemba nawo buku la Salimo anayamba kusirira anthu oipa ndi odzitukumula, osati chifukwa choti ankafuna kuchita zoipa koma ankaona ngati anthu amenewo zinthu zinkawayendera bwino. (Sal. 73:2-9, 11-14) Ankaoneka ngati anali ndi chilichonse, chuma, moyo wabwino komanso analibe nkhawa. Mleviyu anafunika kumaona zinthu monga mmene Yehova amazionera. Atachita zimenezi anakhalanso ndi mtendere ndipo ankasangalala. Iye anati: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha [Yehova].” (Sal. 73:25) Choncho ifenso tisamasirire anthu oipa omwe akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino. Chimwemwe chawo ndi chakanthawi ndipo sadzakhala ndi moyo wosatha. (Mlal. 8:12, 13) Tikamawasirira tingathe kufooka ndiponso tingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho mukayamba kuona kuti mwayamba kusirira anthu oipa, muzichita zimene Mleviyu anachita. Muzimvera malamulo a Mulungu komanso muzikhala pafupi ndi anthu amene amachita zimene Yehova amafuna. Ndipotu mungakhale osangalala kwambiri mukamakonda Yehova kuposa china chilichonse. Komanso mungapitirizebe kuyenda panjira ya ‘kumoyo weniweniwo.’—1 Tim. 6:19. w20.12 19 ¶14-16
Lamlungu, January 23
Pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa, koma mzimu umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza.—Aroma 8:26.
Mukamamufotokozera Yehova nkhawa zanu m’pemphero musamaiwalenso kumuthokoza. Muyenera kumaganizira zinthu zabwino zimene iye wakuchitirani, ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto. Ngati nthawi zina mumalephera kupeza mawu abwino oti mufotokozere mmene mukumvera, muzikumbukira kuti Yehova akhoza kumva pemphero lanu ngakhale litangokhala lonena kuti: ‘Chonde ndithandizeni.’ (2 Mbiri 18:31) Muzidalira nzeru za Yehova osati nzeru zanu. Cha m’ma 700 B.C.E., Ayuda ankaopa kuti akhoza kuukiridwa ndi Asuri. Chifukwa choti sankafuna kukhala pansi pa ulamuliro wankhanza wa Asuriwo, iwo anayamba kupempha thandizo kwa Aigupto. (Yes. 30:1, 2) Yehova anawachenjeza kuti ngati atapitiriza kudalira Aigupto zinthu sizidzawayendera bwino. (Yes. 30:7, 12, 13) Kudzera mwa mneneri Yesaya, iye anauza Ayudawo zimene angachite kuti apeze chitetezo chenicheni. Iye anawauza kuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”—Yes. 30:15b. w21.01 3-4 ¶8-9
Lolemba, January 24
Ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000.—Chiv. 7:4.
Yohane anaona abale ake a Khristu odzozedwa akulandira mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwawo n’kukhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Yesu kumwamba. (Chiv. 20:6) Yehova, Yesu komanso angelo onse adzasangalala kuona Akhristu odzozedwa okwana 144,000 akulandira mphoto yawo kumwamba. Pambuyo pofotokoza za mafumu ndi ansembe 144,000 amenewa, mtumwi Yohane anaona chinthu china chosangalatsa. Iye anaona “khamu lalikulu,” lomwe lidzapulumuke pa Aramagedo. Mosiyana ndi gulu loyamba lija, gulu lachiwirili linali ndi anthu ambiri komanso osawerengeka. (Chiv. 7:9, 10) Iwo anali “atavala mikanjo yoyera,” kutanthauza kuti anali ‘opanda banga’ m’dziko la Satanali ndipo anali okhulupirika kwa Mulungu ndi Khristu. (Yak. 1:27) Anthuwa ankafuula kuti apulumutsidwa chifukwa cha zimene Yehova ndi Yesu, yemwe ndi Mwanawankhosa wa Mulungu, anachita. Komanso iwo anali atanyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo, kutanthauza kuti amavomereza mosangalala kuti Yesu ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.—Yerekezerani ndi Yohane 12:12, 13. w21.01 15-16 ¶6-7
Lachiwiri, January 25
Kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.—2 Sam. 22:36.
Mwamuna angakhale mutu wabwino akamatsanzira mmene Yehova ndi Yesu amachitira pa nkhani yotsogolera. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yehova amachitira pa nkhani ya kudzichepetsa. iye ndi wanzeru kuposa wina aliyense. Komabe, amamvetsera maganizo a atumiki ake. (Gen. 18:23, 24, 32) Iye amalola amene akuwatsogolera kufotokoza maganizo awo. (1 Maf. 22:19-22) Yehova ndi wangwiro, koma samayembekezera kuti anthufe tizichita zinthu popanda kulakwitsa kalikonse. M’malomwake, iye amathandiza atumiki ake omwe si angwiro kuti zinthu ziziwayendera bwino. (Sal. 113:6, 7) Ndipotu Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndi “m’nthandizi” wathu. (Sal. 27:9; Aheb. 13:6) Mfumu Davide ananena kuti anakwanitsa kugwira ntchito yaikulu imene anapatsidwa chifukwa chakuti Yehova ndi wodzichepetsa ndipo anamuthandiza. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Iye anasambitsa mapazi a ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankamuona kuti ndi Ambuye. Yesu ananena kuti: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yoh. 13:12-17) Ngakhale kuti iye anali ndi udindo waukulu, sankafuna kuti ena azimutumikira. M’malomwake iye ndi amene ankatumikira ena.—Mat. 20:28. w21.02 3-4 ¶8-10
Lachitatu, January 26
Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.—Miy. 20:29.
Pali zambiri zimene abale achinyamatanu mungachite. Ambiri a inu muli ndi mphamvu komanso thanzi labwino. Mumachita zambiri pothandiza abale ndi alongo anu mumpingo. Ndipo n’kutheka kuti mumafuna mutakhala mtumiki wothandiza koma mwina mungaganize kuti ena azikuonani kuti ndinu wamng’ono komanso simunafike popatsidwa ntchito zofunika kwambiri. Ngakhale kuti ndinu wachinyamata, pali zambiri zimene mungachite panopa zomwe zingathandize kuti anthu ena mumpingo azikudalirani komanso kukulemekezani. Kodi abale achinyamatanu, muli ndi luso linalake lomwe lingathandize ena mumpingo? Ambiri a inu muli ndi maluso osiyanasiyana. Mwachitsanzo, mwina mumaona kuti achikulire amayamikira akasonyezedwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zawo zamakono pophunzira Baibulo pawokha komanso pamisonkhano. Ndiye mungathandize achikulirewa chifukwa mumadziwa zambiri zokhudza zipangizo zamakono. Pa chilichonse chimene mukuchita, muziyesetsa kusangalatsa Atate wanu wakumwamba. w21.03 2 ¶1, 3; 7 ¶18
Lachinayi, January 27
Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Ngakhale kuti mkazi angakhale wophunzira kuposa mwamuna wake, ndi udindo wa mwamunayo kutsogolera banja lake pa kulambira kwa pabanja komanso pa zinthu zina zokhudza kulambira. (Aef. 6:4) Mkazi ayenera kugonjera mwamuna wake, koma ayenera kudziwa kuti ndi udindo wake kulimbitsa chikhulupiriro chake. Kuti zimenezi zitheke, iye ayenera kumapeza nthawi yophunzira mawu a Mulungu payekha komanso kuganizira mozama zimene waphunzirazo. Zimenezi zingamuthandize kuti azikonda komanso kulemekeza Yehova ndiponso kuti azigonjera mwamuna wake mosangalala. Akazi amene amagonjera amuna awo chifukwa chakuti amakonda Yehova, amakhala osangalala komanso okhutira kusiyana ndi akazi amene amakana kutsatira zimene Yehova anakonza zoti mwamuna azitsogolera m’banja. Akazi ogonjerawa, amaperekanso chitsanzo chabwino kwa anyamata ndi atsikana. Amathandizanso kuti anthu m’banja komanso mumpingo azikondana ndiponso azikhala mwa mtendere. (Tito 2:3-5) Masiku ano, chiwerengero chachikulu cha atumiki a Yehova ndi akazi.—Sal. 68:11. w21.02 13 ¶21-23
Lachisanu, January 28
Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.—Yak. 4:8.
Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yochita zinthu molimba mtima komanso kupirira. Nthawi zina iye ankafooka koma ankatha kupirira chifukwa ankadalira Yehova kuti azimupatsa mphamvu. (2 Akor. 12:8-10; Afil. 4:13) Ifenso tingapeze mphamvu komanso kuchita zinthu molimba mtima ngati modzichepetsa timazindikira kuti timafunika Yehova kuti atithandize. (Yak. 4:10) Tingakhale otsimikiza kuti mayesero amene timakumana nawo si chilango chochokera kwa Yehova. Wophunzira Yakobo ananena kuti: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yak. 1:13) Tikatsimikizira kuti zimene Yakobo ananenazi ndi zoona, timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi. Yehova “sasintha.” (Yak. 1:17) Iye anathandiza Akhristu a m’nthawi ya atumwi pa mayesero amene ankakumana nawo ndipo amatithandizanso masiku ano. Tizipempha Yehova mochokera pansi pamtima kuti atithandize kupeza nzeru, chikhulupiriro komanso kuti atithandize kukhala olimba mtima. Iye adzayankha mapemphero athu. Tikatero tidzakhala otsimikiza kuti iye adzatithandiza kukhalabe osangalala pamene tikupirira mayesero amene tikukumana nawo. w21.02 31 ¶19-21
Loweruka, January 29
Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.—Miy. 27:17.
Mungalimbikitse wophunzira Baibulo yemwe amabwera kumisonkhano mukamamusonyeza chidwi. (Afil. 2:4) Popanda kulowerera pa nkhani zake zaumwini, mungamuyamikire pa zimene wakwanitsa kusintha, mungamufunse mmene phunziro la Baibulo likuyendera, zokhudza banja lake komanso ntchito yake. Izi zingathandize kuti mukhale mabwenzi apamtima komanso kuti wophunzirayo apite patsogolo n’kufika pobatizidwa. Wophunzira Baibulo akayamba kupita patsogolo komanso kusintha zinthu pa moyo wake, muzimuthandiza kuona kuti amawerengeredwa mumpingo. Mungachite zimenezi pomuitanira kunyumba kuti mudzacheze naye. (Aheb. 13:2) Wophunzira Baibulo akavomerezedwa kukhala wofalitsa, mungamamutenge popita mu utumiki. Wofalitsa wina wa ku Brazil, dzina lake Diego, ananena kuti: “Abale ambiri ankanditenga akamapita mu utumiki. Izi zinandithandiza kuti ndiwadziwe bwino. Ndikamayenda nawo ndinkaphunzira zambiri ndipo ndinkaona kuti ndili pa ubwenzi ndi Yehova komanso Yesu.” w21.03 12 ¶15-16
Lamlungu, January 30
Musabwezere choipa pa choipa.—Aroma 12:17.
Yesu anauza otsatira ake kuti azikonda adani awo. (Mat. 5:44, 45) Kodi zimenezi ndi zophweka? Ayi ndithu. Koma mzimu woyera wa Mulungu ungatithandize kuti tikwanitse kuchita zimenezi. Makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa akuphatikizapo chikondi, kuleza mtima, kukoma mtima, kufatsa komanso kudziletsa. (Agal. 5:22, 23) Makhalidwe amenewa amatithandiza kupirira anthu ena akamadana nafe. Anthu ambiri omwe poyamba anali otsutsa, anasintha chifukwa amuna awo, akazi awo, ana awo kapena oyandikana nawo nyumba ankasonyeza makhalidwe amenewa. Ndipo ena mwa anthu amene ankatsutsawo, panopa ndi abale ndi alongo athu. Choncho ngati zimakuvutani kuti muzikonda anthu amene amadana nanu chifukwa chotumikira Yehova, muzipemphera kwa iye kuti akupatseni mzimu woyera. (Luka 11:13) Ndipo muzikhulupirira kuti kumvera Mulungu nthawi zonse n’kofunika kwambiri. (Miy. 3:5-7) Chidani chingakhale chopweteka ndiponso champhamvu koma chikondi ndi champhamvu kwambiri kuposa chidani. Tikamakonda ena, akhoza kusintha n’kusiya kutitsutsa ndipo izi zingachititse kuti Yehova azisangalala. Ngakhale otsutsa atapitiriza kudana nafe, tikhoza kumakhalabe osangalala. w21.03 23 ¶13; 24 ¶15, 17
Lolemba, January 31
Pali mtundu umene walowa m’dziko langa. Mtunduwo ndi wamphamvu ndipo anthu ake ndi osawerengeka.—Yow. 1:6.
Mneneri Yoweli ankalosera za gulu lankhondo. (Yow. 2:1, 8, 11) Yehova ananena kuti adzagwiritsa ntchito ‘gulu lake lankhondo lamphamvu’ (asilikali a ku Babulo) kuti alange Aisiraeli osamvera. (Yow. 2:25) M’pomveka kuti asilikaliwa akutchedwa “mdani wa kumpoto” chifukwa choti Ababulo analowa mu Isiraeli kuchokera kumpoto. (Yow. 2:20) Ndipo gulu lankhondolo likuyerekezeredwa ndi dzombe. Pofotokoza za asilikaliwa, Yoweli ananena kuti: “Amayendabe ngati mwamuna wamphamvu amene akuyenda panjira yake . . . Iwo amathamangira m’mizinda. . . . Amakwera nyumba ndipo amalowa m’nyumbamo kudzera pawindo ngati mbala.” (Yow. 2:8, 9) Tangoganizirani mmene zinalili. Asilikali anali paliponse ndipo panalibe malo obisala. Panalibe munthu amene akanatha kuthawa lupanga la Ababulo. Ababulo (kapena kuti Akasidi) analowa ngati dzombe mumzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E. Baibulo limanena kuti: “Mfumu ya Akasidi, . . . sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu.”—2 Mbiri 36:17. w20.04 5 ¶11-12