Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es22 tsamba 17-26
  • February

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • February
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
  • Timitu
  • Lachiwiri, February 1
  • Lachitatu, February 2
  • Lachinayi, February 3
  • Lachisanu, February 4
  • Loweruka, February 5
  • Lamlungu, February 6
  • Lolemba, February 7
  • Lachiwiri, February 8
  • Lachitatu, February 9
  • Lachinayi, February 10
  • Lachisanu, February 11
  • Loweruka, February 12
  • Lamlungu, February 13
  • Lolemba, February 14
  • Lachiwiri, February 15
  • Lachitatu, February 16
  • Lachinayi, February 17
  • Lachisanu, February 18
  • Loweruka, February 19
  • Lamlungu, February 20
  • Lolemba, February 21
  • Lachiwiri, February 22
  • Lachitatu, February 23
  • Lachinayi, February 24
  • Lachisanu, February 25
  • Loweruka, February 26
  • Lamlungu, February 27
  • Lolemba, February 28
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
es22 tsamba 17-26

February

Lachiwiri, February 1

Modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.​—Afil. 2:3.

Tiziyesetsa kuti tiwadziwe bwino abale ndi alongo athu. Tizicheza nawo misonkhano isanayambe komanso ikatha, tiziyenda nawo mu utumiki ndipo ngati n’kotheka, tiziwaitanira chakudya. Mukatero mwina mudzadabwa kuona kuti mlongo amene amaoneka ngati wosachezeka ali ndi vuto la manyazi, m’bale amene amaoneka ngati wokonda ndalama ali ndi mtima wochereza kapena banja limene limachedwa kumisonkhano limatsutsidwa. (Yobu 6:29) N’zoona kuti tiyenera kupewa ‘kulowerera nkhani za eni.’ (1 Tim. 5:13) Koma ndi bwino kudziwa zinthu zina zokhudza abale ndi alongo athu komanso zimene akumana nazo pa moyo wawo. Mukamudziwa bwino Mkhristu amene sakusangalatsani mukhoza kuyamba kumuchitira chifundo. Pamafunika khama kuti tiwadziwe bwino abale ndi alongo athu. Koma tikamatsatira malangizo a m’Baibulo akuti tifutukule mitima yathu timatsanzira Yehova amene amakonda anthu “kaya akhale a mtundu wotani.”​—1 Tim. 2:3, 4; 2 Akor. 6:11-13. w20.04 16-17 ¶10-12

Lachitatu, February 2

Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.​—Yoh. 15:13.

Pa usiku wake womaliza, Yesu anakumbutsa otsatira ake kuti azikondana. Iye ankadziwa kuti kukhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena n’kumene kukanawathandiza kukhala ogwirizana komanso kupirira anthu ena akamadana nawo. Taganizirani chitsanzo cha mpingo wa ku Tesalonika. Kungochokera pamene mpingowu unakhazikitsidwa, Akhristu a mumpingowo ankangokhalira kuzunzidwa. Koma iwo anakhalabe zitsanzo zabwino pa nkhani yopirira komanso kusonyeza chikondi. (1 Ates. 1:3, 6, 7) Paulo anawalimbikitsa kuti apitirize kusonyeza chikondi “mowonjezereka.” (1 Ates. 4:9, 10) Chikondi chikanawathandiza kuti azilimbikitsa a mtima wachisoni komanso kuthandiza ofooka. (1 Ates. 5:14) Akhristuwo anatsatira malangizo a Paulowa chifukwa m’kalata yake yachiwiri, imene anawalembera patatha pafupifupi chaka, iye anawauza kuti: “Chikondi cha aliyense wa inu kwa mnzake chikuwirikiza.” (2 Ates. 1:3-5) Choncho, chikondi chinawathandiza kupirira mavuto komanso kuzunzidwa. w21.03 22 ¶11

Lachinayi, February 3

Tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.​—Aheb. 12:1.

Kuti tikalandire mphoto ya moyo wosatha, tiyenera kutsatira njira ya moyo wa Chikhristu. (Mac. 20:24; 1 Pet. 2:21) Koma Satana ndi anthu amene amamutsatira amafuna kuti tisiye njirayi n’kuyamba ‘kumathamanga nawo limodzi.’ (1 Pet. 4:4) Iwo amanyoza njira imene timatsatira ndipo amanena kuti njira yawo ndi yabwino komanso yopereka ufulu. Koma zimenezi ndi zabodza. (2 Pet. 2:19) Kusankha njira yolondola n’kofunika kwambiri. Satana amafuna kuti tisiye kuthamanga panjira yopanikiza ‘yolowera ku moyo’ n’kuyamba kuyenda pamsewu waukulu umene anthu ambiri m’dzikoli akuyendamo. Anthu ambiri amakonda msewu umenewu ndipo ndi wosavuta kuyendamo koma “ukupita kuchiwonongeko.” (Mat. 7:13, 14) Choncho kuti tikhalebe panjira yolondola popanda kusokonezeka, tiyenera kudalira Yehova ndiponso kumumvera. w20.04 26 ¶1; 27 ¶5, 7

Lachisanu, February 4

Ndikuchonderera nonse kuti muzipereka mapembedzero kwa Mulungu, muzipereka mapemphero, muzipemphererana, . . . kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira.​—1 Tim. 2:1, 2.

M’zaka zaposachedwa, dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo analowanso mu “dziko lokongola.” (Dan. 11:41) Kodi anachita bwanji zimenezi? Mu 2017, mfumu ya kumpoto yatsopanoyi, inaletsa ntchito ya anthu a Yehova ndi kumanga abale ndi alongo athu ena. Inaletsanso mabuku athu kuphatikizapo Baibulo la Dziko Latsopano. Komanso inalanda ofesi yathu ya nthambi ya ku Russia, Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano. Zimenezi zitachitika, mu 2018 Bungwe Lolamulira linanena kuti dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo ndi mfumu ya kumpoto. Komabe anthu a Yehova salimbana ndi boma lililonse kapena kuyesa kuti alisinthe ngakhale pamene akuzunzidwa kwambiri. M’malomwake iwo amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti azipempherera “anthu onse apamwamba,” makamaka pamene anthuwo akusankha zochita pa nkhani zomwe zingakhudze ufulu wakulambira. w20.05 14 ¶9

Loweruka, February 5

Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.​—1 Tim. 4:16.

Makolo, kuti ana anu atsimikizire kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi choonadi, ayenera kumakonda kwambiri Mulungu komanso kukhulupirira kuti zimene amaphunzira m’Baibulo ndi zoona. Kuti muthandize ana anu kukonda choonadi, muyenera kumawasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yophunzira Baibulo. Muyeneranso kumaganizira mozama zimene mukuphunzira. Mukamachita zimenezi m’pamene mungakwanitse kuthandiza ana anuwo kuti azikonda choonadi. Makolo muyenera kuthandiza ana anu kudziwa mmene angafufuzire nkhani zina akamaphunzira, ngati mmene mumachitira ndi anthu ena amene mumawaphunzitsa Baibulo. Mukatero, mungathandize anawo kuti azikonda Yehova komanso kuti azikhulupirira kuti iye amagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu. (Mat. 24:45-47) Musamangophunzitsa ana anu mfundo zoyambirira za choonadi. Koma muziwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba powaphunzitsanso zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu mogwirizana ndi msinkhu komanso nzeru zawo.​—1 Akor. 2:10. w20.07 11 ¶10, 12-13

Lamlungu, February 6

Pakuti munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.​—Miy. 3:32.

Kodi ndi anthu angati masiku ano omwe akusangalala kukhala pa ubwenzi ndi Yehova? Alipo mamiliyoni ambiri. Tikutero chifukwa padziko lonse pali amuna, akazi komanso ana ambiri amene akuchita zinthu zosonyeza kuti ndi mabwenzi a Mulungu. Anthuwa amakhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa amakhulupirira nsembe ya Yesu. Chifukwa cha nsembeyi, timatha kudzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Tikachita zinthu zofunika zimenezi, timakhala m’gulu la Akhristu mamiliyoni amene nawonso anadzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa, ndipo akusangalala kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, yemwe ndi wamkulu kuposa wina aliyense. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona ubwenzi wathu ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali? Mofanana ndi Abulahamu komanso Yobu, omwe anakhala okhulupirika kwa Mulungu kwa zaka zoposa 100, nafenso tiyenera kukhalabe okhulupirika ngakhale titamutumikira kwa zaka zambiri m’dziko lakaleli. Mofanana ndi Danieli, nafenso tiziona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuposa moyo wathu. (Dan. 6:7, 10, 16, 22) Yehova angatithandize kuti tipirire mayesero aliwonse amene tingakumane nawo n’kupitirizabe kukhala naye pa ubwenzi wolimba.​—Afil. 4:13. w20.05 27 ¶5-6

Lolemba, February 7

Ndipatseni mtima wosagawanika.​—Sal. 86:11.

Mfumu Davide anaona mkazi wina dzina lake Batiseba akusamba. Mkaziyu anali wa mwiniwake. Iye ankadziwa lamulo la Yehova lakuti: “Usalakelake mkazi wa mnzako.” (Eks. 20:17) Koma n’zachidziwikire kuti iye anapitirizabe kuyang’anitsitsa mkaziyo. Apatu mtima wake unagawanika. Anafunika kusankha kusangalatsa Yehova kapena kupitirizabe kulakalaka mkaziyo. Ngakhale kuti kwa nthawi yaitali Davide ankaopa komanso kukonda Yehova, pa nthawiyi anangotsatira zofuna za mtima wake mpaka anachita zinthu zoipa kwambiri. Zimenezi zinanyozetsa dzina la Mulungu. Komanso anapweteketsa anthu a m’banja lake ndiponso anthu ena osalakwa. (2 Sam. 11:1-5, 14-17; 12:7-12) Yehova anapereka chilango kwa Davide. Ndipo Davide anakhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (2 Sam. 12:13; Sal. 51:2-4, 17) Davide sanaiwale mavuto omwe anakumana nawo atasiya kukhala ndi mtima wosagawanika. Kodi Yehova anamuthandizanso kuti akhale ndi mtima wosagawanika? Inde. Tikutero chifukwa Mawu a Yehova amanena za Davide kuti ‘anatumikira Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.’​—1 Maf. 11:4; 15:3. w20.06 11 ¶12-13

Lachiwiri, February 8

Ndinali kuwakoka mokoma mtima ndi mwachikondi.​—Hos. 11:4.

Baibulo limafotokoza kuti chikondi cha Yehova chili ngati chingwe. N’chifukwa chiyani chikondi cha Mulungu chimayerekezeredwa ndi chingwe? Taganizirani izi: Yerekezerani kuti mukumira ndipo wina wakuponyerani chovala chokuthandizani kuti muziyandama. N’zosakayikitsa kuti mungamuyamikire kwambiri. Koma ngati madziwo ndi ozizira kwambiri, chovalacho sichingakuthandizeni kuti mukhalebe ndi moyo. Ndiye mungafunike kuti wina akuponyereni chingwe n’kukukokerani m’boti. Monga mmene Yehova ananenera m’mawu a mulemba laleroli, iye anapitiriza ‘kukoka mokoma mtima ndi mwachikondi’ Aisiraeli omwe anasochera. Umu ndi mmene Mulungu amachitiranso ndi anthu amene anasiya kumutumikira komanso akukumana ndi mavuto ambiri omwe amawadetsa nkhawa. Iye amafuna kuti anthuwo adziwe kuti amawakonda komanso amafuna kuwathandiza kuti abwerere kwa iye. Ndipo Yehova akhoza kugwiritsa ntchito inuyo powathandiza kuti aone chikondi chake. Tizitsimikizira anthu amene anasiya kusonkhana kuti Yehova amawakonda kwambiri komanso tiziwasonyeza kuti nafenso timawakonda. w20.06 27 ¶12-13

Lachitatu, February 9

Wodala ndi munthu wopirira mayesero.​—Yak. 1:12.

Wophunzira Sitefano ataphedwa, Akhristu ambiri anathawa ku Yerusalemu ndipo “anabalalikira m’zigawo za Yudeya ndi Samariya,” moti ena anakafika mpaka kumadera akutali ngati ku Kupuro ndi ku Antiokeya. (Mac. 7:58–8:1; 11:19) Kunena zoona, ophunzirawo anakumana ndi mavuto ambiri. Komabe kulikonse kumene iwo ankapita, ankalalikira uthenga wabwino mofunitsitsa ndipo anakhazikitsa mipingo m’madera ambiri omwe anali pansi pa ufumu wa Roma. (1 Pet. 1:1) Pambuyo pa zimenezi Akhristuwo anakumananso ndi mavuto ena ambiri. Mwachitsanzo, cha m’ma 50 C.E., Mfumu Kalaudiyo analamula kuti Ayuda achoke ku Roma. Choncho Ayuda omwe anakhala Akhristu anakakamizika kusiya nyumba zawo n’kusamukira kumadera ena. (Mac. 18:1-3) Cha m’ma 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu anzake ankatonzedwa poyera poikidwa m’ndende komanso kulandidwa katundu. (Aheb. 10:32-34) Mofanana ndi anthu onse, Akhristu nawonso ankapirira mavuto osiyanasiyana ngati umphawi komanso matenda.​—Aroma 15:26; Afil. 2:25-27. w21.02 26-27 ¶2-4

Lachinayi, February 10

Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.​—Chiv. 12:12.

Tikamayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu, Satana komanso anthu ake sangatilepheretse kuyendabe m’choonadi. (2 Yoh. 8, 9) Akhristufe tiyenera kumayembekezera kuti dzikoli likhoza kudana nafe. (1 Yoh. 3:13) Yohane ananena kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Pamene mapeto akuyandikira, Satana ndi wokwiya kwambiri. Choncho akumagwiritsa ntchito njira zosaonekera monga kukonda chiwerewere kapena mabodza a ampatuko. Nthawi zinanso angachititse kuti anthu azitizunza kwambiri. Satana akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa ndipo akuyesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti alepheretse ntchito yathu yolalikira kapena kuwononga chikhulupiriro chathu. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti ntchito yathu ndi yoletsedwa m’mayiko ena. Ngakhale zili choncho, abale ndi alongo athu a m’mayiko amenewa akupitirizabe kupirira. Abalewa akusonyeza kuti palibe chimene Satana angachite kuti atilepheretse kukhala okhulupirika kwa Yehova. w20.07 24 ¶12-13

Lachisanu, February 11

Mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.​—Aroma 6:23.

Yehova ankafuna kuti anthu azikhala ndi moyo mpaka kalekale m’dziko lokongola limene analenga. Koma Adamu ndi Hava atachimwira Atate wawo wachikondiyu, sakanakhalanso ndi moyo wosatha ndipo iwo limodzi ndi ana awo ankayenera kufa. (Aroma 5:12) Ndiye kodi Yehova anachita chiyani? Nthawi yomweyo, anafotokoza zimene adzachite kuti apulumutse anthu. (Gen. 3:15) Yehova anakonza zoti adzapereke Mwana wake nsembe kuti ana a Adamu ndi Hava adzawomboledwe ku uchimo ndi imfa. Zimenezi ndi zomwe zinachititsa kuti zikhale zotheka kuti aliyense amene wasankha kumutumikira adzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Akor. 15:21, 22) Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake kuukitsa anthu amene anamwalira, koma sitingayembekezere kuti onse adzaukitsidwa nthawi imodzi. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa ngati anthu onse ataukitsidwa nthawi imodzi, ndiye kuti chiwerengero cha anthu chingachuluke kwambiri pa nthawi imodzi ndipo izi zingachititse kuti pakhale chisokonezo. Komatu paja Yehova sangachite zinthu zachisokonezo. Iye amadziwa kuti zinthu zimafunika kuchitika mwadongosolo kuti anthu azikhala mwamtendere.​—1 Akor. 14:33. w20.08 14 ¶3; 15 ¶5

Loweruka, February 12

Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.​—1 Tim. 4:16.

Wophunzira Baibulo ayenera kudziwa kuti cholinga chathu n’choti timuthandize kuti akhale wa Mboni za Yehova. Pali zambiri zimene wophunzira Baibulo ayenera kuchita kuti afike pobatizidwa. Choyamba, ayenera kudziwa Yehova, kumukonda komanso kumukhulupirira. (Yoh. 3:16; 17:3) Kenako wophunzirayo amayamba kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso abale ndi alongo mumpingo. (Aheb. 10:24, 25; Yak. 4:8) Pakapita nthawi, amasiya makhalidwe oipa amene ankachita n’kulapa machimo ake. (Mac. 3:19) Komanso amayamba kuuza ena zimene amakhulupirira. (2 Akor. 4:13) Kenako amadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. (1 Pet. 3:21; 4:2) Limenelitu limakhala tsiku losangalatsa kwambiri kwa aliyense. Wophunzira akamayesetsa kuchita zinthu zimene akuyenera kuchita kuti abatizidwe, tizimuyamikira kuchokera pansi pa mtima ndipo tizimulimbikitsa kuti apitirize kuchita zimenezo. w20.10 17-18 ¶12-13

Lamlungu, February 13

Ngati phazi linganene kuti: “Popeza sindine dzanja, sindili mbali ya thupi,” chimenecho si chifukwa chopangitsa phazi kusakhala mbali ya thupi.​—1 Akor. 12:15.

Mukamadziyerekezera ndi ena mumpingo mungayambe kudziona kuti ndinu osafunika. Anthu ena mumpingo amaphunzitsa mwaluso, ndi adongosolo kapena amadziwa kulimbikitsa ena. Mwina mumaona kuti mulibe luso lochita zinthu ngati mmene iwo amachitira. Zimenezi zingasonyeze kuti ndinu odzichepetsa. (Afil. 2:3) Koma muyenera kukhala osamala. Ngati mumangokhalira kudziyerekezera ndi anthu ena omwe amachita bwino kwambiri zinthu zina, mukhoza kukhumudwa. Monga mmene Paulo ananenera, mungamadzione kuti ndinu osafunika mumpingo. Yehova anapereka mphatso za mzimu woyera kwa Akhristu ena a munthawi ya atumwi, koma mphatso zimene analandirazi sizinali zofanana. (1 Akor. 12:4-11) Yehova anawapatsa mphatso komanso maluso osiyanasiyana komabe Mkhristu aliyense anali wofunika. Masiku ano sitilandira mphatso za mzimu woyera zomwe zingatithandize kuchita zinthu zodabwitsa. Koma mfundo yake ingatithandize. Tingakhale ndi maluso osiyana koma tonsefe ndi amtengo wapatali kwa Yehova. w20.08 23 ¶13-15

Lolemba, February 14

Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.​—Sal. 118:6.

Mukapempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima, iye adzayankha mapemphero anu ndipo sadzakusiyani. (Mac. 4:29, 31) Nthawi zonse iye ndi wokonzeka kukuthandizani. Muziganizira mmene anakuthandizirani pa nthawi imene munkakumana ndi mavuto. Musamaiwale kuti anakupatsani mphamvu kuti muthe kusintha moyo wanu. Sitikukayikira kuti Mulungu amene anaolotsa anthu ake pa Nyanja Yofiira, angakuthandizeni kuti mukhale wophunzira wa Khristu. (Eks. 14:13) Muzikhulupirira kwambiri Yehova ngati mmene ankachitira wamasalimo yemwe ananena mawu amene ali mulemba lalerowa. Yehova akhozanso kuthandiza ofalitsa atsopano kuti akhale olimba mtima. Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Tomoyo. Tsiku limene anayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba anakumana ndi munthu wovuta. Atangowaona, munthuyo anakalipa kuti: “Sindifuna kuti a Mboni za Yehova azibwera pakhomo panga pano.” Kenako anamenyetsa chitseko. Tomoyo sanachite mantha moti anauza mnzake amene anayenda naye kuti: “Wamva zimene munthu uja wanena? Sindinalankhule chilichonse koma anazindikira kuti ndine wa Mboni za Yehova. Zimenezi zandisangalatsa kwambiri.” Panopa Tomoyo ndi mpainiya wokhazikika. w20.09 6 ¶13-14

Lachiwiri, February 15

Asa anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.​—2 Mbiri 14:2.

Asa anauza anthu kuti Yehova ndi amene ‘anawapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira.’ (2 Mbiri 14:6, 7) Iye sankaona kuti nthawi ya mtendereyi inali nthawi yoti azingosangalala. M’malo mwake anayamba kumanga mizinda, mipanda, nsanja komanso mageti. Iye anauza anthu a ku Yuda kuti: “Malo m’dzikoli akadalipo.” Kodi Asa ankatanthauza chiyani? Iye ankatanthauza kuti m’dzikolo munalibe adani omwe akanawalepheretsa kuti aziyenda komanso kumanga mwaufulu. Iye analimbikitsa anthuwo kuti agwiritse ntchito bwino nthawi ya mtendereyi. Asa anagwiritsanso ntchito nthawi ya mtendereyi powonjezera gulu lake la nkhondo. (2 Mbiri 14:8) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sankadalira Yehova? Ayi. M’malomwake, Asa ankadziwa kuti ndi udindo wake monga mfumu kuthandiza anthu kuti akonzekere mavuto amene akanabwera m’tsogolo. Iye ankadziwa kuti mtendere womwe unalipowo sudzakhalapo mpaka kalekale ndipo n’zimene zinachitikadi. w20.09 15 ¶4-5

Lachitatu, February 16

Musapitirire zinthu zolembedwa.​—1 Akor. 4:6.

Chifukwa choti mkulu amasamalira mpingo, mwina akhoza kumaona kuti abale ndi alongo ali ngati ana ake. Komabe pali kusiyana pakati pa udindo umene akulu ali nawo ndi udindo umene amuna omwe ndi mitu ya mabanja ali nawo. Mwachitsanzo, Yehova anapereka kwa akulu udindo woweruza komanso wochotsa munthu aliyense amene wachita tchimo koma osalapa. (1 Akor. 5:11-13) Yehova anapereka kwa mitu ya mabanja udindo wina umene sanaupereke kwa akulu. Iye anapatsa mwamuna udindo wopanga malamulo komanso kuwonetsetsa kuti aliyense m’banja lake akuwatsatira. (Aroma 7:2) Mwachitsanzo, iye ali ndi ufulu wokhazikitsa nthawi imene ana ake ayenera kufika pakhomo madzulo. Alinso ndi mphamvu yopereka chilango kwa anawo ngati atalephera kumvera lamuloli. (Aef. 6:1) Komatu mwamuna wabwino amayamba wakambirana kaye ndi mkazi wake asanakhazikitse malamulo m’banja mwawo, pajatu awiriwa ndi “thupi limodzi.”​—Mat. 19:6. w21.02 16-18 ¶10-13

Lachinayi, February 17

[Nzeru] n’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali, ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo.—Miy. 3:15.

Chinthu china chimene chimachititsa kuti choonadi cha m’Mawu a Mulungu chikhale chamtengo wapatali ndi choti Yehova amachiulula kwa anthu odzichepetsa komanso amene ali ndi “maganizo abwino.” (Mac. 13:48) Anthu odzichepetsawa amavomereza kuti kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi amene amatiphunzitsa mfundo za m’Baibulo masiku ano. (Mat. 11:25; 24:45) Sitingathe kumvetsa Baibulo popanda kuthandizidwa ndipo palibe chinthu chamtengo wapatali kuposa kumvetsa mfundo za m’Baibulo. (Miy. 3:13) Yehova watipatsanso mwayi wophunzitsa ena choonadi chokhudza iyeyo komanso zolinga zake. (Mat. 24:14) Uthenga umene timalalikira ndi wamtengo wapatali, chifukwa umathandiza anthu kukhala m’banja la Yehova komanso umawathandiza kuti adzapeze moyo wosatha. (1 Tim. 4:16) Ndiye kaya timakwanitsa kuchita zambiri mu utumiki kapena ayi, tikuthandiza pa ntchito yofunika kwambiri imene ikuchitika masiku ano. (1 Tim. 2:3, 4) Ndi mwayi waukulu kukhala antchito anzake a Mulungu.​—1 Akor. 3:9. w20.09 26-27 ¶4-5

Lachisanu, February 18

Tinapeza abale ndipo anatichonderera kuti tikhale nawo.​—Mac. 28:14.

Pa ulendo wake wopita ku Roma, kawirikawiri Paulo ankathandizidwa ndi Yehova kudzera mwa okhulupirira anzake. Mwachitsanzo, anzake awiri a Paulo okhulupirika omwe ndi Alisitako ndi Luka, anaganiza zopita naye limodzi ku Roma. Zikuoneka kuti Yesu sanatsimikizire amuna awiri amenewa kuti akafika bwinobwino ku Roma. Komabe mofunitsitsa iwo anaika moyo wawo pangozi kuti apite limodzi ndi Paulo. Zoti apulumuka anazidziwa mkati mwa ulendo wawo pamene anakumana ndi mphepo yamkuntho. Atafika padoko ku Sidoni, Yuliyo analola Paulo “kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalire.” (Mac. 27:1-3) Pambuyo pake atafika mumzinda wa Potiyolo, Paulo ndi anzakewo ‘anapeza abale ndipo anawachonderera kuti akhale nawo masiku 7.’ Pamene abalewo ankasamalira Paulo ndi anzakewo, mosakayikira Paulo ayenera kuti ankasangalatsa abalewo powafotokozera nkhani zolimbikitsa.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 15:2, 3. w20.11 15-16 ¶15-17

Loweruka, February 19

Kukhala wodzipereka kwa Mulungu . . . kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwerawo.​—1 Tim. 4:8.

Makolo, ana anu aziona kuti mumakonda kwambiri Yehova kudzera mu zolankhula komanso zochita zanu. Muzikumbukira kuti mphatso yayikulu imene mungapatse ana anu ndi kuwathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Ndipo chinthu chamtengo wapatali chimene mungawachitire ndi kuwaphunzitsa kuti nthawi zonse azipemphera, aziphunzira Mawu a Mulungu, azisonkhana komanso azilalikira. (1 Tim. 6:6) N’zoona kuti mumafunika kupezera ana anu zinthu zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Komabe muzikumbukira kuti ndalama kapena katundu sizingathandize ana anu kuti adzapulumuke dziko la Satanali likamadzawonongedwa. Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi komwe kungawathandize kuti adzalowe m’dziko latsopano la Mulungu. (Ezek. 7:19) N’zosangalatsa kuona kuti makolo ambiri a Chikhristu amayesetsa kuthandiza ana awo akuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ana a m’mabanja amenewa akakula amapitirizabe kutsatira zimene makolo awo anawaphunzitsa ndipo sasiya kutumikira Yehova komanso sanong’oneza bondo.​—Miy. 10:22. w20.10 28-29 ¶10-11

Lamlungu, February 20

Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.​—Mat. 16:22.

Nthawi zina Mtumwi Petulo ankanena komanso kuchita zinthu zimene ananong’oneza nazo bondo. Mwachitsanzo, pamene Yesu ankauza atumwi ake kuti ayenera kuzunzidwa komanso kuphedwa, Petulo ananena zili pamwambazi. (Mat. 16:21-23) Koma Yesu anamudzudzula. Pamene gulu la anthu linabwera kudzagwira Yesu, Petulo anachita zinthu mopupuluma. Iye anadula khutu la kapolo wa mkulu wa ansembe. (Yoh. 18:10, 11) Apanso Yesu anadzudzula mtumwiyu. Kuwonjezera pamenepo, Petulo anadzitama kuti ngakhale atumwi onse atathawa n’kumusiya Yesu, iyeyo sangachite zimenezo. (Mat. 26:33) Koma Petulo sanali wolimba mtima ngati mmene ankaganizira chifukwa usiku womwewo anachita mantha kwambiri moti anakana katatu kuti sankamudziwa Yesu. Petulo anakhumudwa kwambiri “ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.” (Mat. 26:69-75) N’kutheka kuti iye ankaganiza kuti mwina Yesu sangamukhululukire. Komabe Petulo sanafooke kwambiri mpaka kufika posiya kutumikira Yehova. Pambuyo pake anapitirizabe kutumikira Yehova limodzi ndi atumwi enawo.​—Yoh. 21:1-3; Mac. 1:15, 16. w20.12 20 ¶17-18

Lolemba, February 21

Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino, ndi kuwapatsa ulemu monga chiwiya chosalimba.​—1 Pet. 3:7.

Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja, angasonyeze kuti ndi wodzichepetsa m’njira zambiri. Mwachitsanzo, iye sayembekezera kuti mkazi ndi ana ake azichita zinthu mosalakwitsa chilichonse. Iye amamvetsera maganizo a anthu a m’banja lake ngakhale pamene maganizo awo akusiyana ndi maganizo ake. Kuwonjezera pamenepo, mwamuna wodzichepetsa amakhala wofunitsitsa kugwira ntchito za pakhomo ngakhale kuti m’dera limene amakhala, anthu ambiri amaganiza kuti ntchito za pakhomo ndi za akazi. Zimenezitu zingakhale zovuta kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Mlongo wina dzina lake Rachel ananena kuti: “Kudera limene ndimachokera, mwamuna akamathandiza mkazi wake kutsuka mbale kapena kukonza m’nyumba, achibale komanso anthu oyandikana nawo nyumba amakayikira ngati alidi ‘mwamuna weniweni.’ Iwo amaganiza kuti mwamuna woteroyo mkazi wake sangamamumvere.” Ngati kudera limene mumakhala anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa, muzikumbukira kuti Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake, ngakhale kuti imeneyi inkaonedwa kuti ndi ntchito ya akapolo. Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja wabwino safuna kuti ena azimuona kuti ndi wamphamvu kapena wofunika kwambiri. M’malomwake iye amafuna kuti mkazi ndi ana ake azisangalala. w21.02 2 ¶3; 4 ¶11

Lachiwiri, February 22

Pali chinthu chimodzi chimene ndikuchita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.—Afil. 3:13, 14.

Kukumbukira zinthu zabwino ndi mphatso yochokera kwa Yehova. Koma kaya moyo wathu unali wabwino bwanji m’mbuyomo, tizikumbukira kuti moyo wabwino kwambiri tidzakhala nawo m’dziko latsopano. Anthu ena angatikhumudwitse koma tikasankha kukhululuka, maganizo athu onse amakhala pa kutumikira Yehova. Kudziimba kwambiri mlandu kungatilepheretse kuti tizitumikira Yehova mosangalala. Koma mofanana ndi mtumwi Paulo tizikhulupirira kuti Yehova anatikhululukira. (1 Tim. 1:12-15) Tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha. M’dziko latsopano sitidzadziimbanso mlandu chifukwa cha zinthu zimene tinachita m’mbuyomo. Baibulo limanena kuti nthawi imeneyo: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso.” (Yes. 65:17) Taganizirani mfundo iyi: Ena a ife takalamba tikutumikira Yehova, koma m’dziko latsopano tidzakhalanso anyamata. (Yobu 33:25) Choncho tisamaganizire kwambiri zinthu zakale. M’malomwake, tiziganizira kwambiri za dziko latsopano ndi kuchita zonse zimene tingathe kuti tidzapezekemo. w20.11 24 ¶4; 29 ¶18-19

Lachitatu, February 23

Ndinaona khamu lalikulu la anthu  . . Iwo anapitirizabe kufuula ndi mawu okweza, kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu . . . ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chiv. 7:9, 10.

Kodi tikuyembekezera chiyani kutsogoloku? Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzatipulumutsa modabwitsa pazochitika ziwiri. Choyamba, iye adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika pa nthawi imene adzachititse mafumu a dzikoli kuwononga Babulo Wamkulu, yemwe ndi ufumu wa zipembedzo zonse zonyenga. (Chiv. 17:16-18; 18:2, 4) Chachiwiri, iye adzapulumutsa anthu ake pamene azidzawononga anthu onse omwe ali kumbali ya Satana pankhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Tikakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, Satana sangatichite chilichonse chomwe chingativulaze mpaka kalekale. Ndipotu ndi iyeyo amene adzawonongedwe kuti asadzakhaleponso mpaka kalekale. (Aroma 16:20) Choncho, valani zida zonse zankhondo ndipo musazivule. Musamayese kumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndi dziko lakeli panokha. Muzithandiza abale ndi alongo anu komanso muzitsatira malangizo a Yehova. Mukamachita zimenezi, mudzakhala otsimikiza kuti Atate wanu wakumwamba, yemwe ndi wachikondi adzakupatsani mphamvu komanso kukutetezani.​—Yes. 41:10. w21.03 30 ¶16-17

Lachinayi, February 24

Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.—Yes. 30:15.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova? Tingatero tikamatsatira malangizo amene amatipatsa. M’Baibulo muli nkhani zambiri zimene zimafotokoza chifukwa chake tiyenera kukhala olimba mtima n’kumadalira Yehova. Mukamaphunzira nkhanizi muziganizira zimene zinathandiza atumiki a Mulungu kupitirizabe kukhala olimba mtima pamene ankatsutsidwa. Mwachitsanzo, pa nthawi imene khoti lalikulu la Ayuda linalamula atumwi kuti asiye kulalikira, iwo sanachite mantha. M’malomwake iwo ananena molimba mtima kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:29) Ngakhale kuti anakwapulidwa, iwo sanatekeseke. Chifukwa chiyani? Iwo ankadziwa kuti Yehova ali kumbali yawo ndipo ankasangalala nawo. Choncho anapitirizabe kulengeza uthenga wabwino. (Mac. 5:40-42) Nayenso Sitefano pa nthawi imene ankaphedwa, ankaoneka kuti sakuchita mantha moti mpaka nkhope yake inafika pooneka “ngati nkhope ya mngelo.” (Mac. 6:12-15) N’chifukwa chiyani iye sankachita mantha? Chifukwa anali wotsimikiza kuti Yehova akusangalala naye. w21.01 4 ¶10-11

Lachisanu, February 25

Iwo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.​—Chiv. 7:14.

Zimenezi zikutanthauza kuti iwo ali ndi chikumbumtima choyera komanso Yehova amasangalala nawo. (Yes. 1:18) Iwowa ndi Akhristu odzipereka omwe anabatizidwa komanso amakhulupirira kwambiri nsembe ya Yesu ndipo ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Yoh. 3:36; 1 Pet. 3:21) N’chifukwa chake Yehova amasangalala nawo ndipo iwo amamuchitira “utumiki wopatulika usana ndi usiku” pano padziko lapansi. (Chiv. 7:15) Panopa iwo amagwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu chifukwa amaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri. (Mat. 6:33; 24:14; 28:19, 20) A khamu lalikulu omwe adzapulumuke pa chisautso chachikulu, ndi otsimikiza kuti Mulungu adzapitiriza kuwasamalira chifukwa “wokhala pampando wachifumuyo, adzatambasulira hema wake pamwamba pawo kuti awateteze.” Lonjezo la Mulungu limene takhala tikuliyembekezera kwa nthawi yaitali lidzakwaniritsidwa. Lonjezoli limati: Iye “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.”​—Chiv. 21:3, 4. w21.01 16 ¶9-10

Loweruka, February 26

Ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera.​—Mac. 2:17.

Timasangalala kukhala m’banja la Yehova ndipo timalemekeza zimene Yehova anakonza zoti ena azitsogolera. Baibulo limasonyeza kuti Yehova amaona kuti akazi ndi amtengo wapatali mofanana ndi amuna. Mwachitsanzo, limafotokoza kuti mu nthawi ya atumwi Yehova anapereka mzimu woyera kwa amuna ndi akazi omwe, kuti onse azitha kuchita zodabwitsa monga ngati kulankhula zinenero zosiyanasiyana. (Mac. 2:1-4, 15-18) Ndipotu Yehova anadzoza onsewa ndi mzimu woyera kuti akalamulire limodzi ndi Khristu. (Agal. 3:26-29) Yehova adzaperekanso mphoto ya moyo wosatha kwa amuna ndi akazi padziko lapansi. (Chiv. 7:9, 10, 13-15) Komanso onse amuna ndi akazi, anapatsidwa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Ndipo buku la Machitidwe limatifotokozera ntchito imene mlongo wina dzina lake Purisikila anagwira. Iye limodzi ndi mwamuna wake Akula anathandiza munthu wina wophunzira kwambiri dzina lake Apolo kumvetsa choonadi molondola.​—Mac. 18:24-26. w21.02 14 ¶1; 15 ¶4

Lamlungu, February 27

Mukhale tcheru ndi kuyang’anira gulu lonse la nkhosa, . . . muwete mpingo wa Mulungu.​—Mac. 20:28.

Akulu muli ndi udindo waukulu wothandiza ofalitsa kuti azikhala aluso mu utumiki komanso pochititsa maphunziro a Baibulo. Ngati wofalitsa akuchita manyazi kuchititsa phunziro lake muli pompo, mungadzipereke kuchititsa phunzirolo. Akulu angachite zambiri pothandiza komanso kulimbikitsa ofalitsa amene ali ndi maphunziro a Baibulo. (1 Ates. 5:11) Ngakhale zitakhala kuti panopa tilibe phunziro la Baibulo, tingathandize winawake kupita patsogolo mpaka kubatizidwa. Tikakhala nawo paphunziro la Baibulo la munthu wina, tisamalankhule kwambiri. Ndipo ngati takonzekera bwino, ndemanga zathu zingathandize mwiniwake wa phunzirolo kufotokoza bwino mfundo za m’phunzirolo. Tingathenso kupanga ophunzirawo kukhala anzathu akabwera ku Nyumba ya Ufumu komanso tiziwapatsa chitsanzo chabwino. Akulu angalimbikitsenso ophunzira popeza nthawi yocheza nawo. Angalimbikitsenso ofalitsa amene ali ndi maphunziro a Baibulo powaphunzitsa komanso kumawayamikira. Kunena zoona, timakhalatu osangalala kwambiri tikachita zinazake pothandiza munthu wina kuti ayambe kukonda komanso kutumikira Atate wathu, Yehova. w21.03 13 ¶18-19

Lolemba, February 28

Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.​—Sal. 25:14.

Davide anasonyeza kuti anali munthu wodalirika. Mwachitsanzo, ali wachinyamata iye ankachita khama posamalira nkhosa za bambo ake. Nthawi zina ntchito imeneyi inkakhala yoopsa. Davide anauza Mfumu Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala m’busa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwera mkango komanso chimbalangondo moti chilichonse mwa zilombo zimenezi chinagwira nkhosa ya m’gululo. Pamenepo ine ndinatsatira chilombocho n’kuchipha, ndipo ndinapulumutsa nkhosa mkamwa mwake.” (1 Sam. 17:34, 35) Davide ankaona kuti ndi udindo wake kusamalira nkhosa. Abale achinyamata angatsanzire Davide ngati amachita khama pogwira ntchito iliyonse imene apatsidwa. Davide ali wachinyamata anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ubwenzi umenewu unali wofunika kwambiri kuposa kulimba mtima kwa Davide kapenanso luso limene anali nalo loimba zeze. Sikuti iye ankangoona Yehova monga Mulungu wake koma ankamuonanso monga mnzake weniweni. Choncho abale achinyamatanu, chinthu chofunika kwambiri chimene muyenera kuchita ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Atate wanu wakumwamba. w21.03 3 ¶4-5

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena