March
Lachiwiri, March 1
Ndinu odala anthu akamadana nanu.—Luka 6:22.
Sitimachita kusankha kuti anthu azidana nafe komanso kutizunza chifukwa cha zimene timakhulupirira. Ndiye n’chifukwa chiyani timasangalala ena akamadana nafe? Pali zifukwa zitatu. Choyamba, tikapirira timakhala ovomerezeka pamaso pa Mulungu. (1 Pet. 4:13, 14) Chachiwiri, chikhulupiriro chathu chimayengedwa ndipo zikatero chimalimba kwambiri. (1 Pet. 1:7) Ndipo chachitatu, tidzapeza mphoto yamtengo wapatali, yomwe ndi moyo wosatha. (Aroma 2:6, 7.) Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yesu anaukitsidwa, atumwi anayamba kuona chimwemwe chimene Yesu anawafotokozera. Atawakwapula n’kuwalamula kuti asiye kulalikira, iwo anasangalala. Chifukwa chiyani? “Chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:40-42) Iwo ankakonda kwambiri Mbuye wawo kuposa mmene ankaopera anthu amene ankadana nawo. Ndipo anasonyeza chikondi chawo popitiriza kulalikira uthenga wabwino “mwakhama.” Abale athu ambiri masiku ano, akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Iwo amadziwa kuti Yehova sadzaiwala ntchito yawo komanso chikondi chomwe amasonyeza pa dzina lake. w21.03 25 ¶18-19
Lachitatu, March 2
Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.—Mlal. 3:11.
Akhristu odzozedwa sabadwa ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba. Mulungu ndi amene amawapatsa chiyembekezochi. Iwo amaganizira za chiyembekezo chawochi, kuchipempherera, komanso amakhala ofunitsitsa kukalandira mphoto yawo kumwamba. Iwo sadziwa n’komwe kuti adzakhala ndi matupi otani akadzapita kumwambako. (Afil. 3:20, 21; 1 Yoh. 3:2) Ngakhale zili choncho, amayembekezera kukakhala pamalo awo mu Ufumu wakumwamba. A nkhosa zina mwachibadwa amasangalala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. Iwo amayembekezera mwachidwi nthawi imene adzathandize kukonza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso. Amalakalaka nthawi imene adzamange nyumba, kulima minda komanso kulera ana awo ali angwiro. (Yes. 65:21-23) Akuyembekezeranso kudzapita malo osiyanasiyana padzikoli kukaona mapiri, nkhalango, nyanja komanso kuphunzira zinthu zonse zimene Yehova analenga. Koposa zonse, a nkhosa zina amasangalala kwambiri kudziwa kuti adzapitirizabe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. w21.01 18-19 ¶17-18
Lachinayi, March 3
Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona . . . mpaka zonse zinawonongedwa.—2 Mbiri 36:19.
Ababulo atamaliza kuwononga, anthu akanatha kungonena kuti: “Dziko ili ndi bwinja, lopanda munthu wokhalamo kapena nyama yoweta. Linaperekedwa m’manja mwa Akasidi.” (Yer. 32:43) Patapita zaka 200 kuchokera pamene Yoweli analemba ulosi wake, Yehova anagwiritsa ntchito Yeremiya kuti alosere zinthu zina zokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Iye ananena kuti Aisiraeli amene ankachita zoipa adzafufuzidwa kwambiri mpaka kugwidwa. Ulosiwu umati: “‘Inetu ndikuitana asodzi ambiri,’ watero Yehova, ‘ndipo adzawawedza. Kenako ndidzaitana anthu ambiri osaka nyama, ndipo adzawasaka m’phiri lililonse, pachitunda chilichonse, ndi m’mapanga a m’matanthwe. . . . Ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse ndi machimo awo onse.’” Ngakhale nyanja kapena nkhalango sizikanatha kubisa Aisiraeli osalapawa kwa asilikali a ku Baibulo.—Yer. 16:16, 18. w20.04 5 ¶12-13
Lachisanu, March 4
Iye [Loti] anali kuzengereza.—Gen. 19:16.
Pa nthawi ina yovuta kwambiri, Loti ankazengereza kutsatira malangizo a Yehova. Angelo awiri anafika n’kumuuza kuti iye ndi banja lake achoke mu Sodomu. N’chifukwa chiyani anamuuza zimenezi? Iwo anati: “Malo ano tiwawononga.” (Gen. 19:12, 13) Tsiku lotsatira, Loti ndi banja lake anali asanachokebe. Choncho angelo anamuchenjezanso koma Loti ‘ankazengerezabe.’ Mwina tingaone kuti Loti anali wamphwayi kapenanso wosamvera. Koma Yehova sanasiye kumuthandiza. Baibulo limati: “Mwa chifundo cha Yehova pa iye,” angelo anagwira dzanja iyeyo, mkazi wake, ndi ana ake aakazi awiriwo, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda. (Genesis 19:15, 16) N’kutheka kuti panali zifukwa zambiri zochititsa Yehova kuti achitire chifundo Loti. Mwina Loti ankazengereza kuchoka chifukwa choopa anthu okhala kunja kwa mzindawo. Koma panali zinthu zinanso zoopsa. Loti ayenera kuti ankadziwa za mafumu amene anagwera m’maenje aphula omwe anali m’chigwa chapafupi ndi mzindawo. (Gen. 14:8-12) N’zosachita kufunsa kuti Loti ankadera nkhawa mkazi wake komanso ana ake. Kuwonjezera pamenepa, Loti anali wachuma choncho n’kutheka kuti anali ndi nyumba yapamwamba ku Sodomu. (Gen. 13:5, 6) N’zoona kuti zimenezi sizinali zifukwa zomveka zoti Loti alephere kumvera Yehova mwamsanga. Koma Yehova sanaganizire kwambiri zimene Loti analakwitsa ndipo ankamuonabe kuti ndi “munthu wolungama.”—2 Pet. 2:7, 8. w20.04 18 ¶13-14
Loweruka, March 5
Gulu la achinyamata amene ali ngati mame a m’bandakucha lili pamodzi ndi iwe.—Sal. 110:3.
Achinyamata, dziwani kuti pangatenge nthawi kuti anthu amene anakudziwani muli mwana avomereze kuti tsopano mukukula. Komabe mungakhale wotsimikiza kuti Yehova amaona zambiri osati chabe mmene mukuonekera. Iye amakudziwani bwino kwambiri ndipo amadziwa zimene mungakwanitse kuchita. (1 Sam. 16:7) Choncho muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Davide anachita zimenezi poyang’anitsitsa zimene Yehova analenga komanso kuganizira zimene akuphunzirapo zokhudza Mlengi. (Sal. 8:3, 4; 139:14; Aroma 1:20) Chinthu china chimene mungachite ndi kupempha Yehova kuti azikupatsani mphamvu. Mwachitsanzo, kodi anzanu akusukulu amakusekani kapena kukuvutitsani chifukwa choti ndinu wa Mboni za Yehova? Ngati ndi choncho, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kupirira vutolo. Muzigwiritsa ntchito malangizo othandiza opezeka m’Mawu ake komanso mabuku ndi mavidiyo othandiza pophunzira Baibulo. Mungamakhulupirire kwambiri Yehova mukaona nthawi iliyonse imene wakuthandizani kulimbana ndi mavuto anu. Kuwonjezera apo, anthu ena akaona kuti mumadalira Yehova akhoza kuyamba kukudalirani. w21.03 4 ¶7
Lamlungu, March 6
Pemphero la anthu owongoka mtima limam’sangalatsa [Yehova].—Miy 15:8.
Anthu omwe ndi mabwenzi apamtima amamasukirana kuuzana zakukhosi. Umu ndi mmenenso ziyenera kukhalira pa ubwenzi wathu ndi Yehova. Yehova amatilankhula kudzera m’Mawu ake. Tikamawawerenga timadziwa maganizo ake komanso mmene amamvera. Ifenso timalankhula naye kudzera m’pemphero ndipo tingathe kumufotokozera zimene zili mumtima mwathu komanso mmene tikumvera. Pokhala iye ndi bwenzi lathu lapamtima, amamvetsera ndi kuyankha mapemphero athu. Nthawi zina angayankhe mapemphero athu mofulumira koma pena tingafunike kupitirizabe kupempherera nkhaniyo. Koma timakhala otsimikiza kuti adzatiyankha pa nthawi yake komanso m’njira yoyenera. Zingathekenso kuti yankho limene Mulungu angatipatse lingakhale losiyana ndi lomwe timayembekezera. Mwachitsanzo, mwina m’malo motithetsera mavuto ena ake, angangotipatsa nzeru komanso mphamvu zoti tithe “kuwapirira.”(1 Akor. 10:13) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso yamtengo wapatali yapemphero? Njira ina ndi kutsatira malangizo akuti ‘tizipemphera mosalekeza.’—1 Ates. 5:17. w20.05 27-28 ¶7-8
Lolemba, March 7
Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.—Mat. 24:13.
Anthu othamanga pa mpikisano amayang’ana kwambiri msewu n’cholinga choti asapunthwe. Koma ngati agwa, amadzuka n’kupitiriza kuthamanga. Iwo amaganizira kwambiri zomaliza mpikisanowo n’kukalandira mphoto, osati zimene zawapunthwitsa. Pa mpikisano wathu, timapunthwa nthawi zambiri, kaya polankhula kapena kuchita zinthu zolakwika. Nthawi zina, anzathu amene akuthamanga nafe pampikisanowu ndi amene angatikhumudwitse. Koma zimenezi si zodabwitsa chifukwa tonsefe si angwiro ndipo tikuthamanga limodzi pamsewu wopanikiza wopita ku moyo wosatha. Choncho nthawi zina tikhoza kusokonezana, zomwe zingachititse anzathu kukhala ndi “chifukwa chodandaulira.” (Akol. 3:13) Koma m’malo moganizira zimene zatipunthwitsa, tiziganizira kwambiri za mphoto imene tidzalandire n’kupitiriza kuthamanga. Tikakwiya n’kumakana kudzuka, sitingamalize nawo mpikisanowu ndipo sitingalandire mphoto. Komanso ngati tikukana kudzuka tikhoza kupunthwitsa anthu ena omwe akuyesetsa kuthamanga pamsewu wopanikiza wopita ku moyowu. w20.04 26 ¶1; 28 ¶8-9
Lachiwiri, March 8
Ufumuwo . . . udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo.—Dan. 2:44.
Mneneri Danieli anafotokoza za chifaniziro chachikulu chimene thupi lake linapangidwa ndi zitsulo zosiyanasiyana. Mbali iliyonse ya chifanizirochi imaimira maboma osiyanasiyana omwe analamulira madera amene anthu a Mulungu ankakhala. Mabomawa analamulira pa nthawi zosiyanasiyana. Mapazi a chifanizirochi omwe anali achitsulo chosakanizika ndi dongo akuimira ulamuliro womaliza wa Britain ndi America. Ulosiwu ukutanthauza kuti ulamulirowu udzakhala ukulamulirabe pamene Ufumu wa Mulungu uzidzawononga maboma onse a anthu. Mtumwi Yohane nayenso anafotokoza za maulamuliro amphamvu padziko lonse omwe analamulira anthu a Yehova. Iye anayerekezera maulamulirowa ndi chilombo cha mitu 7. Mutu wa 7 wa chilombochi umaimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Mfundo imeneyi ndi yofunika chifukwa ikutithandiza kudziwa kuti sipakubweranso mutu wina. Mutu umenewu ndi womwe udzakhale ukulamulira mpaka pamene Khristu ndi asilikali ake adzauwononge limodzi ndi chilombochi.—Chiv. 13:1, 2; 17:13, 14. w20.05 14 ¶11-12
Lachitatu, March 9
Mulungu ndiye chikondi.—1 Yoh. 4:8.
Mawu amenewa amatikumbutsa mfundo yofunika kwambiri ya choonadi yakuti: Mulungu ndi amene analenga moyo komanso ndi mwiniwake wa chikondi. Yehova amatikonda kwambiri ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tiziona kuti ndife otetezeka, tizikhala osangalala komanso okhutira. Akhristu sachita kusankha kuti asonyeze chikondi kapena ayi chifukwa limeneli ndi lamulo. (Mat. 22:37-40) Tikamudziwa bwino Yehova, ndi pamene zimakhala zosavuta kumvera lamulo loyamba. Izi zili choncho chifukwa choti Yehova ndi wangwiro, amatiganizira komanso amachita nafe zinthu mokoma mtima. Koma mwina zingativute kumvera lamulo lachiwiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa abale ndi alongo athu, omwe ali m’gulu la anzathu amene tiyenera kuwakonda, si angwiro. Nthawi zina akhoza kulankhula kapena kuchita zinthu m’njira yosonyeza kuti sanatiganizire. Yehova ankadziwa kuti tidzakumana ndi mavuto ngati amenewa, choncho anauzira anthu ena kuti alembe malangizo ofotokoza chifukwa chake tiyenera kusonyezana chikondi komanso mmene tingachisonyezere. Ndipo mmodzi wa anthuwa anali mtumwi Yohane.—1 Yoh. 3:11, 12. w21.01 8 ¶1-2
Lachinayi, March 10
Satana asatichenjerere.—2 Akor. 2:11.
Kaya tangoyamba kumene kutumikira Yehova kapena tamutumikira kwa zaka zambiri, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimayesetsa kupewa mayesero a Satana amene angachititse kuti ndikhale ndi mtima wogawanika?’ Mwachitsanzo, kodi mumatani mukaona chithunzi pa TV kapena pa intaneti chimene chingakuchititseni kuyamba kuganizira zinthu zolakwika? Mwina zingakhale zosavuta kuganiza kuti sikuti chithunzicho kapena filimuyo ndi yolaula. Koma kodi mwina ingakhale njira ya Satana yofuna kukulepheretsani kukhala ndi mtima wosagawanika? Zimenezi tingaziyerekezere ndi nkhwangwa imene munthu amagwiritsira ntchito akafuna kuwaza nkhuni. Powazapo mbali yakuthwa yankhwangwayo ndi imene imalowa m’chikunicho. Ndiyeno mbali yakuthwayo ikamalowa, chikunicho chimawazika. Zithunzi ndi mafilimuwo zingakhale ngati mbali yakuthwa yankhwangwa. Zinthu zowoneka ngati zazing’ono komanso zabwinobwino, zikhoza kuchititsa munthu kuti achite tchimo lomwe lingamulepheretse kukhala ndi mtima wosagawanika komanso kumulepheretsa kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Choncho tiyenera kupewa choipa chilichonse kulowa mumtima mwathu, kuti tipitirize kuopa Yehova ndi kukhala ndi mtima wosagawanika. w20.06 11-12 ¶14-15
Lachisanu, March 11
Kunyamula zofooka za osalimba.—Aroma 15:1.
Mofanana ndi mwana wolowerera wa mufanizo la Yesu, anthu ofooka akhoza kumavutika maganizo. (Luka 15:17-24) Komanso n’kutheka kuti zimene akumana nazo m’dziko la Satanali zachititsa kuti asakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti alimbitsenso chikhulupiriro chawo. Mufanizo la nkhosa imene inasochera, Yesu anafotokoza kuti m’busa ananyamula nkhosayo paphewa pake ndi kupita nayo komwe kunali zinzake. M’busayo anali atathera nthawi yaitali komanso mphamvu zake poifufuza. Komabe ataipeza anaona kuti ikufunika kunyamulidwa chifukwa inalibe mphamvu zoti n’kubwerera payokha. (Luka 15:4, 5) Timafunika kugwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zathu pothandiza anthu amene anafooka kuti akwanitse kulimbana ndi mavuto amene angawalepheretse kuyambiranso kutumikira Yehova. Koma mzimu wa Yehova, Mawu ake ndiponso mabuku amene timalandira zingatithandize polimbikitsa anthuwa kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Ndiye ngati mwapemphedwa kuti muziphunzira ndi munthu amene anafooka, muziona kuti ndi mwayi wanu. w20.06 28 ¶14-15
Loweruka, March 12
Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.—Yoh.13:35.
Tiyenera kumakondana kuti tisonyeze kuti ndife Akhristu oona. Koma timafunikanso “kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.” (Afil. 1: 9) Kupanda kutero, tikhoza kutengeka ndi “mphepo iliyonse ya chiphunzitso chonyenga cha anthu,” kuphatikizapo ampatuko. (Aef. 4:14) Pamene ophunzira ena a Yesu anasiya kumutsatira, mtumwi Petulo anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri kuti Yesu anali ndi “mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:67, 68) Ngakhale kuti pa nthawiyi Petulo sankamvetsa zonse zokhudza mawu a moyowa, iye anakhalabe wokhulupirika chifukwa ankadziwa kuti Yesu ndi Khristu. N’zotheka kuti nanunso muzikhulupirira kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. Mukatero, chikhulupiriro chanu chidzakhala cholimba kwambiri ndipo mudzathandizanso ena kulimbitsa chikhulupiriro chawo.—2 Yoh. 1, 2. w20.07 8 ¶2; 13 ¶18
Lamlungu, March 13
Ana anga okondedwa, tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.—1 Yoh. 3:18.
Kuti tithandize abale ndi alongo athu kukhalabe m’choonadi, tiyenera kumawasonyeza chifundo. (1 Yoh. 3:10, 11, 16-17) Tiyenera kumakondana osati pamtendere pokha, komanso pamavuto. Mwachitsanzo, kodi mukudziwa m’bale kapena mlongo amene waferedwa ndipo akufunika kutonthozedwa komanso kuthandizidwa m’njira zina? Kapena mwamva zoti okhulupirira anzanu akhudzidwa ndi ngozi zachilengedwe ndipo akufunika kuwamangiranso Nyumba za Ufumu komanso nyumba zawo? Timasonyeza chifundo ndiponso kuti timakonda kwambiri abale athu ndi zochita zathu, osati ndi zolankhula zathu zokha. Tikamakondana timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi. (1 Yoh. 4:7, 8) Njira ina yomwe timasonyezera chikondi ndi kukhululukira ena. Mwachitsanzo, munthu wina angatikhumudwitse, kenako n’kupepesa. Zikatere, tingasonyeze chikondi ngati tingamukhululukire n’kuiwala nkhaniyo.—Akol. 3:13. w20.07 24 ¶14-15
Lolemba, March 14
Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.—Mac. 24:15.
Kodi munthu aliyense woukitsidwa azidzakhala ndi mphunzitsi wakewake ngati mmene zimakhalira ndi maphunziro a Baibulo masiku ano? Kodi anthuwa adzaikidwa m’mipingo n’kuphunzitsidwa kuti nawonso azidzaphunzitsa anthu ena omwe adzaukitsidwe pambuyo pawo? Tingoyembekezera kuti tidzaone pa nthawiyo. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti pofika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yes. 11:9) Mosakayikira tidzakhala ndi ntchito yambiri yosangalatsa m’zaka 1,000 zimenezi. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, anthu onse a Yehova adzafunika kupitirizabe kusintha zinthu pa moyo wawo kuti Yehova azidzasangalala nawo. Choncho onse azidzachitira chifundo anthu amene adzaukitsidwe, powathandiza kuti alimbane ndi makhalidwe oipa n’kumatsatira mfundo za Yehova. (1 Pet. 3:8) Anthu oukitsidwawo adzaona kuti anthu a Yehova ndi odzichepetsa komanso akuyesetsa kusintha kuti azikondweretsa Yehova ndipo nawonso adzakhala ofunitsitsa kuti azimulambira.—Afil. 2:12. w20.08 16 ¶6-7
Lachiwiri, March 15
Aliyense payekha ayese ntchito yake, . . . osati modziyerekezera ndi munthu wina.—Agal. 6:4.
Tikamatsatira malangizo a mtumwi Paulo n’kumaona zimene timachita pa moyo wathu, tingayambe kuona kuti tili ndi maluso amene anthu ena alibe. Mwachitsanzo, mkulu angakhale kuti alibe luso lokamba nkhani koma angakhale ndi luso lothandiza anthu kuyamba kutumikira Yehova. Kapena sachita zinthu mwadongosolo ngati akulu ena koma ndi wokoma mtima ndipo abale ndi alongo amamasuka kumufunsa malangizo a m’Malemba. Kapenanso amakonda kuchereza alendo. (Aheb. 13:2, 16) Tikazindikira zinthu zimene timachita bwino, tingakhale osangalala podziwa kuti pali zimene tingachite mumpingo. Ndipo sitingamachitire nsanje abale amene ali ndi maluso osiyana ndi athu. Kaya timachita zotani mumpingo, tonse tiyenera kukulitsa maluso athu komanso kuchita bwino utumiki umene tapatsidwa. w20.08 24 ¶16-18
Lachitatu, March 16
Ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga.—Chiv. 7:9.
Mu 1935, pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira ku Washington, D.C. ku America, M’bale J. F. Rutherford anakamba nkhani yosaiwalika yamutu wakuti “Khamu Lalikulu.” Munkhaniyi M’bale Rutherford anafotokoza za “khamu lalikulu la anthu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9. Pa nthawiyo Ophunzira Baibulo ankaganiza kuti khamu lalikulu ndi gulu la anthu amene sanali okhulupirika kwenikweni poyerekeza ndi Akhristu odzozedwa koma nawonso adzapita kumwamba. M’bale Rutherford anagwiritsa ntchito Malemba pofotokoza kuti a khamu lalikulu sadzapita kumwamba, koma ndi nkhosa zina za Khristu, omwe ndi anthu amene adzapulumuke pa ‘chisautso chachikulu’ n’kudzakhala padzikoli mpaka kalekale. (Chiv. 7:14) Yesu analonjeza kuti: “Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.” (Yoh. 10:16) Nkhosa zina zimenezi ndi a Mboni za Yehova okhulupirika amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Mat. 25:31-33, 46. w21.01 14 ¶1-2
Lachinayi, March 17
Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa, koma yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.—Mat. 10:22.
Timafunika kupilira kuti tigwire ntchito yathu yolalikira mpaka pamapeto. (Mat. 28:19, 20) Kupirira si khalidwe limene timabadwa nalo. Nthawi zambiri anthufe timafuna kumangochita zinthu zomwe ndi zophweka. Komabe nthawi zina zinthu zofunika kwambiri sizimakhala zophweka. Choncho timafunika kupirira kuti tizichite. N’chifukwa chake timafunika kudziphunzitsa kuti tizitha kuchita zinthu zovuta. Yehova angatithandize kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera. (Agal. 5:22, 23) Mtumwi Paulo anali munthu wopirira. Iye anavomereza kuti ‘ankamenya’ thupi lake kuti azichita zinthu zoyenera. (1 Akor. 9:25-27) Iye analimbikitsanso ena kuti azisonyeza khalidweli komanso kuti azichita zinthu zonse “moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akor. 14:40) Tiyenera kumachita khama kuti tizitumikira Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa anthu nthawi zonse.—Mac. 2:46. w20.09 6-7 ¶15-17
Lachisanu, March 18
M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe.—Maliko 13:10.
M’mayiko ambiri abale athu amagwira ntchito yolalikira mwaufulu. Kodi umu ndi mmene zilili m’dziko lanu? Ngati ndi choncho mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ufulu umenewu ndikuugwiritsa ntchito bwanji?’ Masiku otsiriza ano ndi nthawi yosangalatsa kwa anthu a Yehova, chifukwa iwo akuchita khama kugwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu, yomwe ikupita patsogolo kwambiri. Pali zinthu zambiri zomwe tingachite pogwira ntchito imeneyi. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mwanzeru nthawi imene tili pa mtendere? (2 Tim. 4:2) Mungachite bwino kuona mmene zinthu zilili pa moyo wanu, kapena kusintha zina ndi zina kuti inuyo kapena wina m’banja mwanu, awonjezere zochita mu utumiki, mwina kuchita upainiya. Ino si nthawi yomasonkhanitsa chuma kapena zinthu. Tikutero chifukwa zinthu zimenezi sitingadzapulumuke nazo limodzi pa chisautso chachikulu. (Miy. 11:4; Mat. 6:31-33; 1 Yoh. 2:15-17) Ofalitsa ambiri aphunzira chinenero china kuti azichigwiritsa ntchito polalikira komanso kuphunzitsa anthu. Gulu la Yehova limatipatsa zinthu zambiri zomwe zimatithandiza kuti tizilalikira m’zinenero zoposa 1,000. w20.09 16 ¶9-11
Loweruka, March 19
Upitirize kumenya nkhondo yabwino.—1 Tim. 1:18.
Msilikali wabwino amakhala wokhulupirika. Iye amamenya nkhondo mwamphamvu pofuna kuteteza anthu amene amawakonda komanso zinthu zimene amaziona kuti ndi zamtengo wapatali. Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti akhale wodzipereka kwa Mulungu kapena kuti akhale wokhulupirika kwa Mulungu. (1 Tim. 4:7) Tikamakonda kwambiri Mulungu m’pamenenso timafunitsitsa kugwira mwamphamvu choonadi. (1 Tim. 4:8-10; 6:6) Msilikali wabwino amafunikanso kuchita khama kuti nthawi iliyonse azikhala wokonzeka kumenya nkhondo. Timoteyo anapitirizabe kukhala wolimba mwauzimu chifukwa anatsatira malangizo amene Paulo anamupatsa akuti athawe zilakolako zoipa, ayesetse kukhala ndi makhalidwe abwino komanso azicheza ndi Akhristu anzake. (2 Tim. 2:22) Kuchita zimenezi kumafuna kudziletsa. Timafunika kudziletsa kuti tipambane pankhondo yolimbana ndi zilakolako zathupi. (Aroma 7:21-25) Komanso timafunika kudziletsa kuti tipitirizebe kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano. (Aef. 4:22, 24) Ndiponso pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse timatopa, komabe timafunika kudzikakamiza kuti tikasonkhane.—Aheb. 10:24, 25. w20.09 28 ¶9-11
Lamlungu, March 20
Ndatsimikiza mtima kutsatira malangizo anu, mpaka kalekale, ndithu kwa moyo wanga wonse.—Sal. 119:112.
Tiyenera kukhala oleza mtima tikamathandiza ophunzira Baibulo kuti afike podzipereka n’kubatizidwa. Koma pa nthawi ina, tingafunike kufufuza kuti tidziwe ngati wophunzirayo akufunadi kutumikira Yehova Mulungu. Kodi amasonyeza kuti akuyesetsa kumvera malamulo a Yesu? Kapena kodi amangosangalala ndi kuphunzira Baibulo basi? Nthawi ndi nthawi muziona zimene wophunzira wanu akuchita posonyeza kuti akusintha. Mwachitsanzo, kodi wophunzira wanu amasonyeza kuti amakonda Yehova? Kodi amapemphera kwa Yehova? (Sal. 116:1, 2) Kodi amakonda kuwerenga Baibulo? (Sal. 119:97) Kodi amafika pamisonkhano nthawi zonse? (Sal. 22:22) Kodi wasintha zinthu zina pa moyo wake posonyeza kuti akutsatira zimene akuphunzira? Kodi wayamba kuuza achibale ndi anzake zimene akuphunzira? (Sal. 9:1) Koposa zonse, kodi akufuna kukhala wa Mboni za Yehova? (Sal. 40:8) Ngati wophunzirayo sakusintha, tiyenera kufufuza mosamala chifukwa chake, kenako tingakambirane naye nkhaniyo mokoma mtima komanso mosapita m’mbali. w20.10 18 ¶14-15
Lolemba, March 21
Amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, chifukwa ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.—Yoh. 8:29.
Nthawi zonse Atate ake a Yesu amasankha bwino zochita komanso pamene anali padziko lapansi makolo ake ankasankha zinthu mwanzeru. Komabe Yesu atakula ankafunika kusankha yekha zochita. (Agal. 6:5) Mofanana ndi tonsefe, Yesu nayenso anali ndi ufulu wosankha zochita. Iye akanatha kusankha kuti azingochita zofuna zake osati zimene Mulungu amafuna. Koma m’malomwake, anasankha kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Yesu atadziwa zimene Yehova ankafuna kuti achite, anasankha kuchita zimenezo. (Yoh. 6:38) Iye ankadziwa kuti anthu ambiri adzadana naye ndipo zimenezi zinkamuvutitsa maganizo, komabe anasankha kumvera Yehova. Pamene Yesu anabatizidwa mu 29 C.E., ankaona kuti chofunika kwambiri pa moyo wake n’kuchita zimene Yehova amafuna. (Aheb. 10:5-7) Ndipo ngakhale pamene ankafa pamtengo wozunzikirapo, Yesu sanasiye kuchita zimene Atate ake amafuna.—Yoh. 19:30. w20.10 29 ¶12; 30 ¶15
Lachiwiri, March 22
Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.—Aheb. 13:5.
Kodi mukudziwa abale kapena alongo mumpingo mwanu amene akuvutika chifukwa cha matenda kapena chifukwa chakuti akukumana ndi mavuto ena? Kapena mwina ali ndi chisoni chifukwa chakuti wachibale wawo anamwalira? Tikadziwa kuti munthu wina akufunika thandizo, tingapemphe Yehova kuti atithandize kuti timuuze mawu olimbikitsa kapena kumuchitira zinthu zabwino. N’kutheka kuti zimene tingalankhule kapena kuchita ndi zimene zingalimbikitse m’bale kapena mlongo wathuyo. (1 Pet. 4:10) Timalimba mtima chifukwa tikudziwa kuti Yehova ali nafe. Amatithandiza pogwiritsa ntchito Yesu komanso angelo. Ndipo ngati zikugwirizana ndi chifuniro chake, Yehova angatithandize pogwiritsa ntchito anthu audindo. Komanso malinga ndi zimene zachitikira ambirife, taona kuti Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera polimbikitsa atumiki ake kuti athandize Akhristu anzawo. Mofanana ndi mtumwi Paulo, tili ndi zifukwa zabwino zonenera molimba mtima kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”—Aheb. 13:6. w20.11 17 ¶19-20
Lachitatu, March 23
Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.—Yes. 30:15.
Atumwi anali ndi umboni wokwanira wotsimikizira kuti Yehova anali nawo. Iye anali atawapatsa mphamvu kuti azitha kuchita zodabwitsa. (Mac. 5:12-16; 6:8) Koma umu si mmene zilili ndi ife masiku ano. Yehova satipatsa mphamvu zochita zodabwitsa ngati kale. Koma ngakhale zili choncho, kudzera m’Mawu ake mwachikondi amatitsimikizira kuti ngati titavutika chifukwa cha chilungamo iye amasangalala nafe ndipo mzimu wake umakhala nafe. (1 Pet. 3:14; 4:14) Choncho m’malo moganizira zomwe tidzachite tikamadzazunzidwa m’tsogolo, tiziganizira zimene tiyenera kuchita kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova kuti adzatithandiza komanso kutipulumutsa. Tizikhulupirira lonjezo la Yesu lakuti: “Ndidzakuuzani mawu oti munene ndikukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.” Anatilonjezanso kuti: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” (Luka 21:12-19) Komanso tisamaiwale kuti Yehova amakumbukira ngakhale tinthu ting’onoting’ono tokhudza atumiki ake omwe anamwalira ali okhulupirika n’cholinga choti adzawaukitse. w21.01 4 ¶12
Lachinayi, March 24
Ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.—Mac. 24:15.
Mtumwi Paulo sanali woyamba kufotokoza zokhudza kuuka kwa akufa. Yobu nayenso anafotokozapo za nkhani imeneyi. Iye sankakayikira kuti Mulungu adzamukumbukira n’kumuukitsa kuti akhalenso ndi moyo. (Yobu 14:7-10, 12-15) Nkhani ya “kuuka kwa akufa” ndi mbali ya “maziko” kapena kuti “chiphunzitso choyambirira” pa zonse zimene Akhristu amakhulupirira. (Aheb. 6:1, 2) Paulo anafotokoza za kuuka kwa akufa muchaputala 15 cha buku la 1 Akorinto. Zimene analemba ziyenera kuti zinalimbikitsa Akhristu a mu nthawi yake. Chaputala chimenechi chingatilimbikitsenso ifeyo komanso kulimbitsa chiyembekezo chimene takhala nacho kwa nthawi yaitali. Kuukitsidwa kwa Yesu Khristu kumatithandiza kuti tizikhulupirira kuti achibale athu amene anamwalira kapena ngati ifenso titamwalira tidzaukitsidwa. Nkhani imeneyi inali mbali ya “uthenga wabwino” umene Paulo analengeza kwa anthu a ku Korinto. (1 Akor. 15:1, 2) Ndipotu iye ananena kuti ngati Mkhristu sangakhulupirire kuti Yesu anaukitsidwa ndiye kuti chikhulupiriro chakecho chingakhale chopanda ntchito.—1 Akor. 15:17. w20.12 2 ¶2-4
Lachisanu, March 25
Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja, . . . Ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.—Mat. 26:75.
Kodi n’chiyani chinathandiza mtumwi Petulo? Iye anakumbukira kuti Yesu anali atamupempherera kale kuti chikhulupiriro chake chisathe. Yehova anayankha pemphero la Yesu lochokera pansi pamtimali. Kenako Yesu anaonekera kwa Petulo kuti amulimbikitse. (Luka 22:32; 24:33, 34; 1 Akor. 15:5) Yesu anaonekeranso kwa atumwi onse atagwira ntchito usiku wonse koma osapha nsomba. Panthawiyi Yesu anamupatsa Petulo mwayi winanso womusonyeza mmene amamukondera. Yesu anakhululukira mnzake wapamtimayu ndipo anamupatsa ntchito yambiri. (Yoh. 21:15-17) Mmene Yesu anachitira zinthu ndi Petulo zimasonyeza kuti iye ndi wachifundo kwambiri ngati Atate wake. Choncho tikalakwitsa zinazake, tisamaganize kuti Yehova sangatikhululukire. Tizikumbukira kuti Satana ndi amene amafuna kuti tiziganiza choncho. M’malomwake tizikumbukira kuti Yehova amatikonda komanso amatimvetsa ndipo ndi wokonzeka kutikhululukira. Choncho tiyenera kumutsanzira, anthu ena akachita zinthu zotikhumudwitsa.—Sal. 103:13, 14. w20.12 20-21 ¶17-19
Loweruka, March 26
Ndidzadalira Mulungu.—Sal. 27:3.
Tingaphunzire kanthu pa zitsanzo za anthu ena amene analephera kudalira Yehova. Kuphunzirapo pa zitsanzo zoipa za anthu amenewa kungatithandize kuti ifenso tisadzachite zimene iwo analakwitsa. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Asa anadalira Yehova atakumana ndi mavuto. Koma m’kupita kwa nthawi iye sanadalire Mulungu ndipo ankaona kuti akhoza kuthana nawo yekha. (2 Mbiri 16:1-3, 12) Kwa ena, zimene anachita Asa popempha Asuri kuti amuthandize pamene ankalimbana ndi Aisiraeli zingaoneke ngati zothandiza. Koma zimenezi zinangothandiza kwa kanthawi kochepa. Yehova anauza Mfumu Asa kudzera mwa mneneri kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya, osadalira Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” (2 Mbiri 16:7) Tiyenera kukhala osamala kuti tisamadzidalire n’kumaona kuti tikhoza kuthetsa tokha mavuto, m’malo modalira Yehova kuti atithandize kudzera m’Mawu ake Baibulo. Ngakhale pamene tikufuna kusankha zochita mofulumira, tizichita zinthu mopanda mantha komanso kudalira Yehova, ndipo iye adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. w21.01 6 ¶13-15
Lamlungu, March 27
Iwo sadzamvanso njala.—Chiv. 7:16.
Panopa atumiki ena a Yehova akuvutika ndi njala chifukwa chosowa ndalama zogulira chakudya. Akuvutikanso ndi ziwawa zimene zikuchitika m’mayiko awo komanso nkhondo. Ndiponso ena ali m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupirira. Komabe a khamu lalikulu amasangalala chifukwa chodziwa kuti akadzapulumuka, adzakhala ndi chakudya cha mwanaalirenji komanso azidzalandira malangizo ambiri kuchokera kwa Yehova. Yehova akamadzawononga dziko loipa la Satanali, adzateteza a khamu lalikulu ku mkwiyo wake wotentha womwe adzausonyeze pamitundu ya anthu. Chisautso chachikulu chikadzatha, Yesu adzatsogolera onse opulumuka ku “madzi a moyo” wosatha. (Chiv. 7:17) Tangoganizani, a khamu lalikulu akuyembekezeratu zinthu zosangalatsa kwambiri. Pa anthu mabiliyoni omwe akhalapo ndi moyo padzikoli, anthu amene adzapulumuke pa chisautso chachikuluwa akhoza kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 11:26) A nkhosa zina akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri ndipo amathokoza Yehova ndi Yesu chifukwa cha zimenezi. w21.01 16-17 ¶11-12
Lolemba, March 28
Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani.—2 Ates. 3:3.
Pa usiku wake womaliza kukhala ndi moyo monga munthu, Yesu ankaganizira mavuto omwe ophunzira ake adzakumane nawo. Chifukwa choti ankawakonda kwambiri anzakewa, iye anapempha Yehova kuti ‘awayang’anire kuopera woipayo.’ (Yoh. 17:14, 15) Yesu ankadziwa kuti akangobwerera kumwamba, Satana Mdyerekezi apitiriza kumenya nkhondo ndi onse amene akufuna kutumikira Yehova. Apa n’zoonekeratu kuti anthu a Yehova ankafunika kutetezedwa. Panopa tikufunika kutetezedwa kwambiri ndi Yehova kuposa kale. Satana anachotsedwa kumwamba ndipo “ali ndi mkwiyo waukulu.” (Chiv. 12:12) Iye wachititsa anthu amene amatizunza kuti aziona ngati “akuchita utumiki kwa Mulungu.” (Yoh. 16:2) Ndipo ena omwe sakhulupirira Mulungu amatizunza chifukwa timachita zosiyana ndi anthu a m’dzikoli. Koma kaya amatizunza pa zifukwa zotani, sitimachita mantha. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha zimene zanenedwa mu lemba la leroli. w21.03 26 ¶1, 3
Lachiwiri, March 29
China chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.—Aroma 8:39.
Chilichonse chimene Yehova amachita, amachichita chifukwa cha chikondi. Iye amaonetsetsanso kuti tili ndi zinthu zofunika pa moyo. Ndiponso chifukwa chotikonda, iye anatipatsa dipo. Nayenso Yesu amatikonda kwambiri, moti analolera kupereka moyo wake chifukwa cha ife. (Yoh. 3:16; 15:13) Choncho palibe chimene chingalepheretse Yehova ndi Yesu kusonyeza chikondi kwa anthu amene ndi okhulupirika kwa iwo. (Yoh. 13:1; Aroma 8:35) Mofanana ndi zimenezi, chilichonse chimene mwamuna yemwe ndi mutu wa banja amachita ayenera kuchichita chifukwa cha chikondi. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika kwambiri? Mtumwi Yohane anafotokoza kuti: “Amene sakonda m’bale wake [kapena banja lake], amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:11, 20) Choncho mwamuna yemwe amakonda banja lake ndipo akufuna kutsanzira Yehova ndi Yesu, amayesetsa kuthandiza anthu a m’banjalo kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, kuwathandiza kuti aziona kuti ndi otetezeka komanso amawapezera zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Iye amaphunzitsa ana ake komanso kuwapatsa chilango ngati pakufunika kutero. Nthawi zonse amasankha zochita zimene zingalemekeze Yehova komanso kuthandiza banja lake. w21.02 5 ¶12-13
Lachitatu, March 30
Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.—Sal. 55:22.
Atate wathu wachikondi amadziwa kuti zinthu zoipa zimene zinatichitikira zingatichititse kuti tizidziona ngati opanda pake. Mulungu amaona makhalidwe abwino amene tili nawo ngakhale kuti patokha sitiona kuti tili ndi makhalidwe amenewa. (1 Yoh. 3:19, 20) Munthu wina angakhale kuti amayesetsa kuti asiye kuchita makhalidwe oipa koma angapezeke kuti wachitanso, ndipo zimenezi zingamukhumudwitse. N’zoona kuti mwachibadwa timadziimba mlandu tikalakwitsa zinazake. (2 Akor. 7:10) Koma sitikuyenera kudziimba mlandu mopitirira malire n’kumaganiza kuti: ‘Ndine wachabechabe ndipo Yehova sangandikhululukire.’ Maganizo amenewa ndi olakwika ndipo angapangitse kuti tisiye kutumikira Yehova. M’malomwake muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akukhululukireni n’cholinga choti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Iye. (Yes. 1:18) Iye akaona kuti mwalapa kuchokera pansi pamtima angakukhululukireni. Kuwonjezera pamenepo muyenera kukauzanso akulu. Iwo angakuthandizeni moleza mtima kuti mukhalenso pa ubwenzi ndi Yehova.—Yak. 5:14, 15. w20.12 23 ¶5-6
Lachinayi, March 31
[Uziona] akazi achikulire ngati amayi ako. Akazi achitsikana . . . ngati alongo ako.—1 Tim. 5:2.
Yesu ankalemekeza kwambiri akazi. Yesu sankatengera maganizo a Afarisi omwe ankaona kuti akazi ndi otsika. Afarisi sankalankhula ndi akazi pagulu ngakhale kukambirana nawo mfundo za m’Malemba. Koma Yesu ankakambirana mfundo zofunika za m’Malemba ndi amuna kuphatikizaponso akazi omwe anali ophunzira ake. (Luka 10:38, 39, 42) Iye ankapitanso limodzi ndi akazi kokalalikira. (Luka 8:1-3) Komanso Yesu anapereka mwayi kwa akazi woti akauze atumwi ake kuti iye waukitsidwa. (Yoh. 20:16-18) Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti azilemekeza akazi. Iye ankadziwa kuti amayi ake ndi agogo ake ndi amene anayambirira kumuphunzitsa “malemba oyera.” (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) M’kalata imene analembera Akhristu a ku Roma, Paulo anaperekanso moni kwa alongo pochita kuwatchula mayina. Sikuti Paulo ankangoona utumiki umene alongo ankachita, koma ankawayamikiranso chifukwa cha zimenezi.—Aroma 16:1-4, 6, 12; Afil. 4:3. w21.02 15 ¶5-6