Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es22 tsamba 37-46
  • April

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
  • Timitu
  • Lachisanu, April 1
  • Loweruka, April 2
  • Lamlungu, April 3
  • Lolemba, April 4
  • Lachiwiri, April 5
  • Lachitatu, April 6
  • Lachinayi, April 7
  • Lachisanu, April 8
  • Loweruka, April 9
  • Lamlungu, April 10
  • Lolemba, April 11
  • Lachiwiri, April 12
  • Lachitatu, April 13
  • Lachinayi, April 14
  • TSIKU LA CHIKUMBUTSO
    Dzuwa Litalowa
    Lachisanu, April 15
  • Loweruka, April 16
  • Lamlungu, April 17
  • Lolemba, April 18
  • Lachiwiri, April 19
  • Lachitatu, April 20
  • Lachinayi, April 21
  • Lachisanu, April 22
  • Loweruka, April 23
  • Lamlungu, April 24
  • Lolemba, April 25
  • Lachiwiri, April 26
  • Lachitatu, April 27
  • Lachinayi, April 28
  • Lachisanu, April 29
  • Loweruka, April 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
es22 tsamba 37-46

April

Lachisanu, April 1

Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.​—Aroma 15:4.

Kodi mukukumana ndi mayesero aakulu? N’kutheka kuti mwina munthu wina mumpingo wakukhumudwitsani. (Yak. 3:2) Mwinanso anzanu a kuntchito kapena kusukulu amakunyozani chifukwa chotumikira Yehova. (1 Pet. 4:3, 4) Kapenanso anthu a m’banja lanu amakuletsani kuti musamapite kumisonkhano komanso musamauze ena zimene mumakhulupirira. (Mat. 10:35, 36) Mayesero amene mukukumana nawo akakhala aakulu, mungayambe kuganiza kuti mwina ndi bwino kusiya kutumikira Yehova. Komabe muyenera kukhala otsimikiza kuti ngakhale mutakumana ndi mayesero otani, Yehova adzakupatsani nzeru komanso mphamvu zoti mupirire. M’Mawu ake Yehova anaikamo nkhani za anthu amene si angwiro ndiponso zimene anachita kuti athe kulimbana ndi mayesero amene ankakumana nawo. Iye anachita zimenezi n’cholinga choti tiziphunzirapo kanthu. Zimenezi ndi zomwe anauzira mtumwi Paulo kuti alembe. Tikamawerenga nkhanizi zimatilimbikitsa ndiponso zimatipatsa chiyembekezo. Koma kuti tipindule, pali zambiri zimene tiyenera kuchita osati kungowerenga Baibulo. Tizilola Malemba kuti azisintha mmene timaganizira komanso azitifika pamtima. w21.03 14 ¶1-2

Loweruka, April 2

Muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.​—Yoh. 4:35.

Kodi inuyo mumaona anthu amene mumawalalikira ngati mbewu zofunika kukolola? Ngati mumawaona choncho, zikhoza kukuthandizani m’njira zitatu. Choyamba, mudzalalikira mwakhama kwambiri. Paja nthawi yokolola imakhala yochepa ndipo munthu amafunika kugwira ntchito mwakhama. Chachiwiri, mudzasangalala mukaona anthu akumvetsera uthenga wabwino. Baibulo limanena kuti: ‘Anthu amasangalala pa nthawi yokolola.’ (Yes. 9:3) Ndipo chachitatu, mudzaona kuti munthu aliyense akhoza kukhala wophunzira. Choncho mudzasintha uthenga wanu kuti ugwirizane ndi zimene munthuyo amakonda. N’kutheka kuti otsatira a Yesu ankaona kuti Asamariya ndi okanika koma si mmene Yesu ankawaonera. Iye ankaona kuti akhoza kukhala ophunzira ake. Nafenso tiyenera kuona kuti anthu am’gawo lathu akhoza kukhala ophunzira a Khristu. Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Iye ankadziwa zimene anthu amene ankawalalikirawo amakhulupirira, ankadziwa zimene anthu amakonda ndiponso ankawaona kuti akhoza kukhala ophunzira a Yesu. w20.04 8-9 ¶3-4

Lamlungu, April 3

Manda ndiponso malo a chiwonongeko zili pamaso pa Yehova. Ndiye kuli bwanji mitima ya ana a anthu?—Miy. 15:11.

M’malo moweruza msanga zolinga za munthu, tiyenera kuyesetsa kumumvetsa. Yehova yekha ndi amene amatimvetsa bwino. Choncho tizimupempha kuti azitithandiza kuona anthu ena mmene iye amawaonera komanso kudziwa mmene tingawachitire chifundo. Sitingasankhe kuti abale ndi alongo awa tiziwachitira chifundo, awa ayi. Chifukwa onse amakumana ndi mavuto ambiri ofanana ndi amene Yona, Eliya, Hagara ndi Loti anakumana nawo. Ndi zoona kuti nthawi zina angadzibweretsere okha mavutowo. Koma kunena zoona, ifenso tinachitapo zimenezi nthawi ina. Choncho m’pomveka kuti Yehova amafuna kuti tizichitirana chifundo. (1 Pet. 3:8) Tikamamvera Yehova, timathandiza kuti banja lathu lapadziko lonse likhale logwirizana. Choncho tiyeni tonse tiziyesetsa kumvetsera mwatcheru, kuwadziwa bwino anthu komanso kuwachitira chifundo. w20.04 18-19 ¶15-17

Lolemba, April 4

Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.​—1 Pet. 2:21.

Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yomvera Yehova. Choncho chinthu chofunika kwambiri chomwe tingachite kuti tizimvera Yehova ndi kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri. (Yoh. 8:29) Kuti tipitirize kuyenda m’choonadi, tiyenera kutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wachoonadi ndiponso kuti zonse zimene amatiuza m’Mawu ake ndi zoona. Tiyeneranso kutsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya amene Mulungu analonjeza. Anthu ambiri masiku ano amakaikira kuti Yesu anadzozedwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. M’kalata yake, Yohane anachenjeza kuti kunali “anthu onyenga ambiri” omwe akanatha kusocheretsa anthu amene ankakaikira choonadi chokhudza Yehova komanso Yesu. (2 Yoh. 7-11) Iye analemba kuti: “Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?” (1 Yoh. 2:22) Choncho kuti tisapusitsidwe, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu. Tikamachita zimenezi tingadziwe bwino Yehova komanso Yesu. (Yoh. 17:3) Ndipo zimenezi ndi zomwe zingatipangitse kutsimikizira kuti tikudziwa choonadi. w20.07 21 ¶4-5

Lachiwiri, April 5

Tsimikizani mtima kuti simuikira m’bale wanu . . . chopunthwitsa.​—Aroma 14:13.

Njira ina imene tingapewere ‘kupunthwitsa’ anthu pa mpikisanowu ndi kulolera zimene ena akufuna m’malo moumirira maganizo athu. (Aroma 14:19-21; 1 Akor. 8:9, 13) Pamenepa tingati tikusiyana ndi wothamanga pa mpikisano weniweni yemwe amafuna kuti mphoto ikhale yake basi. Othamanga amenewa amangoganizira zofuna zawo zokha. Choncho angakankhe anthu ena n’cholinga choti iwowo akhale patsogolo. Koma ifeyo sitilimbana pa mpikisanowu. (Agal. 5:26; 6:4) Cholinga chathu n’kuthandiza anthu ambiri kuti akamalize nafe mpikisanowu n’kulandira mphoto ya moyo. Choncho tiziyesetsa kutsatira malangizo akuti “musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afil. 2:4) Yehova walonjeza kuti adzapereka mphoto kwa aliyense amene adzamalize mpikisanowu, kaya ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli. w20.04 28 ¶10; 29 ¶12

Lachitatu, April 6

Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu.—Chiv. 7:14.

Akhristu mamiliyoni ambiri adzapulumuka n’kulowa m’dziko latsopano. Opulumukawo adzaona kugonjetsedwa kwinanso kwa imfa chifukwa anthu mabiliyoni amene anamwalira adzaukitsidwa. Tangoganizirani mmene tidzasangalalire kuona zinthu zodabwitsa zimenezi zikuchitika. (Mac. 24:15) Onse amene adzakhale okhulupirika kwa Yehova adzagonjetsanso imfa imene tinatengera kwa Adamu. Ndipo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Mkhristu aliyense ayenera kusangalala kwambiri ndi mawu olimbikitsa okhudza kuukitsidwa kwa akufa amene Paulo analembera Akhristu a ku Korinto. Tili ndi zifukwa zabwino zomvera malangizo a Paulo akuti tizichita zonse zimene tingathe “mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) Tikamayesetsa kugwira nawo ntchitoyi mwakhama, tingayembekezere kudzasangalala ndi moyo m’tsogolo. Moyo umenewu udzakhala wosangalatsa kwambiri kuposa chilichonse chimene tingachiganizire panopa. Umenewu udzakhala umboni wakuti zonse zimene tikuchita mu ntchito ya Ambuye, sizinapite pachabe. w20.12 13 ¶16-17

Lachinayi, April 7

Magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.​—Chiv. 19:19.

Zikuoneka kuti maulosi opezeka pa Ezekieli 38:10-23; Danieli 2:43-45; 11:44–12:1 ndi Chivumbulutso 16:13-16, 21, amafotokoza zinthu zofanana. Ngati zili choncho, ndiye tikuona kuti pachitika zinthu zotsatirazi. Chisautso chachikulu chikadzangoyamba, “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzapanga mgwirizano wa mayiko. (Chiv. 16:13, 14) Mgwirizano umenewu ndi womwe Malemba amautchula kuti “Gogi wa kudziko la Magogi.” (Ezek. 38:2) Mayikowa adzaukira anthu a Mulungu pofuna kuwawononga kuti asadzapezekenso. Pofotokoza za nthawi imeneyi, mtumwi Yohane analosera kuti matalala aakulu adzagwera adani a Mulungu. N’kutheka kuti matalala aakuluwa akuimira uthenga wachiweruzo umene anthu a Yehova azidzalengeza womwe udzachititse kuti Gogi wa ku Magogi aukire anthu a Mulungu n’cholinga choti awawonongeretu.​—Chiv. 16:21. w20.05 15 ¶13-14

Lachisanu, April 8

Ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.​—Luka 11:13.

Mzimu woyera ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu amatipatsa. Tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri mphatsoyi tikamaganizira zimene ukutithandiza kuchita masiku ano. Yesu asanapite kumwamba, anauza ophunzira ake kuti: “Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Mothandizidwa ndi mzimu woyera, anthu pafupifupi 8.5 miliyoni padziko lonse akulambira Yehova. Komanso monga anthu a Mulungu tikusangalala ndi paradaiso wauzimu chifukwa mzimu wa Mulungu umatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Makhalidwewa ndi monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa komanso kudziletsa. Amenewa ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Kunena zoona mzimu woyera ndi mphatso yamtengo wapatali. w20.05 28 ¶10; 29 ¶13

Loweruka, April 9

Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi.​—1 Akor. 15:21.

Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kunena kuti anthu omwe azidzalandira abale awo azidzatha kuwazindikira. Mwachitsanzo, tikaona zimene Yehova anachita poukitsa anthu ena m’mbuyomu, tingayembekezere kuti adzalenganso anthu amene anamwalirawo m’njira yoti azidzaoneka, kulankhula komanso kuganiza ngati mmene ankachitira asanamwalire. Kumbukirani kuti Yesu anayerekezera imfa ndi tulo ndipo kuukitsidwa anakuyerekezera ndi kudzutsidwa kutulo. (Mat. 9:18, 24; Yoh. 11:11-13) Munthu amene anali mtulo akadzuka, amaoneka komanso kulankhula mofanana ndi mmene amachitira asanagone ndiponso amakumbukira zonse zimene amaganiza asanakagone. Chitsanzo pankhaniyi ndi Lazaro. Iye anali atamwalira kwa masiku 4 ndipo thupi lake linali litayamba kuwola. Koma Yesu atamuukitsa, azichemwali ake anamuzindikira ndipo mosakayikira iyenso anawakumbukira.​—Yoh. 11:38-44; 12:1, 2. w20.08 14 ¶3; 16 ¶8

Lamlungu, April 10

Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.​—Chiv. 7:10.

Sikuti Mulungu amaona kuti odzozedwa ndi osiyana ndi a nkhosa zina. Iye amawakonda onsewa ndipo amaona kuti ndi amtengo wapatali. Ndipotu iye anawagula onsewo pamtengo wofanana, womwe ndi moyo wa Mwana wake wokondedwa. Kusiyana kumene kulipo pakati pa magulu awiriwa ndi kwakuti ali ndi chiyembekezo chosiyana. Koma onse amafunika kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndi Khristu. (Sal. 31:23) Ndipo tizikumbukira kuti mzimu woyera wa Mulungu umagwira ntchito mofanana kwa tonsefe. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amapereka mzimu wake woyera kwa aliyense mogwirizana ndi mmene akufunikira. Yehova wapereka chiyembekezo chabwino cham’tsogolo kwa mtumiki wake aliyense wodzipereka. (Yer. 29:11) Mwambo wokumbukira imfa ya Khristu umatipatsa tonsefe mwayi waukulu wotamanda Mulungu ndi Khristu chifukwa cha zimene anatichitira n’cholinga choti tidzasangalale ndi moyo wosatha. Mpake kuti mwambo wa Chikumbutso umakhala wapadera kwambiri kwa Akhristu chaka chilichonse. w21.01 18 ¶16; 19 ¶19

Lolemba, April 11

Muzichita zimenezi nthawi zonse.​—1 Akor. 11:25.

Anthu ambiri amene amapezeka pa Chikumbutso ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Ndiye n’chifukwa chiyani anthu amenewa amapezeka pamwambowu? Chifukwa chimene amapezekerapo n’chofanana ndi chimene anthu amapezekera pa ukwati wa mnzawo. Anthuwo amafuna kuthandiza komanso kusonyeza kuti amakonda anthu amene akukwatiranawo. Mofanana ndi zimenezi, a nkhosa zina amapezeka pa Chikumbutso chifukwa chofuna kuthandiza komanso kusonyeza kuti amakonda Khristu ndi odzozedwa. Iwo amapezekanso pamwambowu posonyeza kuti amayamikira kwambiri nsembe ya Yesu yomwe inathandiza kuti adzakhale ndi moyo wosatha padzikoli. Chifukwa china chimene chimapangitsa a nkhosa zina kupezeka pamwambo wa Chikumbutso ndi chakuti amafuna kumvera lamulo la Yesu. Pamene Yesu ankayambitsa mwambo wapaderawu limodzi ndi atumwi ake okhulupirika, anawauza kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (1 Akor. 11:23-26) Choncho a nkhosa zina adzapitirizabe kuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa nthawi yonse imene odzozedwa adzakhale adakali ndi moyo padzikoli. w21.01 17-18 ¶13-14

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Yohane 12:12-19; Maliko 11:1-11

Lachiwiri, April 12

Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.​—1 Yoh. 4:9.

Zochita zathu ndi zimene zingasonyeze kuti timakondadi ena. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:17, 26.) Mwachitsanzo, Yehova amatikonda. (1 Yoh. 4:19) Ndipo amatiuza zimenezi kudzera m’Mawu ake Baibulo. (Sal. 25:10; Aroma 8:38, 39) Komabe, timadziwa kuti Mulungu amatikonda osati chabe chifukwa cha mawu amene amatiuzawo, koma chifukwa cha zimene amatichitira. Yehova analola kuti Mwana wake wokondedwa avutike komanso kufa chifukwa cha ife. (Yoh. 3:16) Ndiye kodi pamenepa tingakayikirenso kuti Yehova amatikonda kwambiri? Timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso Yesu tikamawamvera. (Yoh. 14:15; 1 Yoh. 5:3) Ndipotu Yesu anatilamula kuti tizikondana. (Yoh. 13:34, 35) Tisamangosonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu ndi mawu okha. M’malomwake, tizisonyeza kuti timawakonda ndi zochita zathu.​—1 Yoh. 3:18. w21.01 9 ¶6; 10¶8

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Yohane 12:20-50

Lachitatu, April 13

Ndakutchani mabwenzi.​—Yoh. 15:15.

Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera akuyembekezera kudzakhala ndi Yesu kwamuyaya komanso kulamulira naye mu Ufumu wa Mulungu. Iwo adzatha kumuona, kulankhula naye komanso kuchita naye zinthu zina. (Yoh. 14:2, 3) Yesu adzasonyezanso chikondi kwa anthu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli. Ngakhale kuti anthuwo sadzamuona, adzayamba kukhala anzake apamtima kwambiri akamadzasangalala ndi moyo umene Yehova ndi Yesuyo adzawapatse. (Yes. 9:6, 7) Timapeza madalitso ambiri tikamayesetsa kukhala anzake a Yesu. Mwachitsanzo, panopa iye amatisonyeza chikondi ndiponso kutithandiza. Komanso tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. Ndipo koposa zonse, kukhala anzake a Yesu kumatithandiza kupeza mwayi wamtengo wapatali wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate ake, Yehova. Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala anzake a Yesu. w20.04 25 ¶15-16

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Luka 21:1-36

Lachinayi, April 14

Mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.​—1 Akor. 15:22.

Mtumwi Paulo analembera kalatayi Akhristu odzozedwa a ku Korinto amene ankayembekezera kudzaukitsidwa n’kupita kumwamba. Akhristu amenewo ‘anayeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi kuitanidwa kuti akhale oyera.’ Paulo anatchula za “anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu.” (1 Akor. 1:2; 15:18; 2 Akor. 5:17) M’kalata yake ina analemba kuti ‘amene anagwirizana naye [Yesu] pokhala ndi imfa yofanana ndi yake,’ ‘adzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana ndi iye.’ (Aroma 6:3-5) Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu ndipo anapita kumwamba. Zimenezi ndi zomwe zidzachitike kwa onse amene “ali ogwirizana ndi Khristu” kapena kuti Akhristu onse odzozedwa. Paulo analemba kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa n’kukhala “chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” (1 Akor. 15:20) Yesu anali woyamba kuukitsidwa ndi thupi lauzimu n’kupatsidwa moyo wosatha. w20.12 5-6 ¶15-16

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6

TSIKU LA CHIKUMBUTSO
Dzuwa Litalowa
Lachisanu, April 15

Tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.​—1 Ates. 4:17.

Panopa Akhristu odzozedwa akamwalira, nthawi yomweyo amaukitsidwa n’kupita kumwamba. Mawu a mtumwi Paulo a pa 1 Akorinto 15:51, 52, akutsimikizira zimenezi. Abale a Khristuwa akaukitsidwa, amasangalala kwambiri. Baibulo limatiuza ntchito imene anthu amene adzasandulike “m’kuphethira kwa diso,” adzagwire akapita kumwamba. Yesu anawauza kuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo, ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.”​—Chiv. 2:26, 27. w20.12 12 ¶14-15

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Mateyu 26:17-19; Maliko 14:12-16; Luka 22:7-13 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Yohane 13:1-5; 14:1-3

Loweruka, April 16

Khristu anaukitsidwa kwa akufa.​—1 Akor. 15:20.

Ponena kuti Yesu ndi “chipatso choyambirira,” Paulo ankatanthauza kuti pambuyo pake anthu enanso adzaukitsidwa n’kupita kumwamba. Patapita nthawi atumwi ndi ena amene “ali ogwirizana ndi Khristu,” anaukitsidwa n’kupita kumwamba mofanana ndi Yesu. (1 Akor. 15:18) Pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Akhristu a ku Korinto, anthu amene “ali ogwirizana ndi Khristu” anali asanayambe kuukitsidwa n’kupita kumwamba. Paulo anasonyeza kuti zimenezi zidzachitika m’tsogolo. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akor. 15:23; 1 Ates. 4:15, 16) Panopa, tikukhala mu “nthawi ya kukhalapo” kwa Khristu imene Paulo ananenayi. Atumwi komanso Akhristu ena odzozedwa amene anamwalira ankafunika kuyembekezera nthawi ya kukhalapo imeneyi kuti alandire mphoto yawo yakumwamba ndi ‘kugwirizananso ndi Yesu poukitsidwa mofanana ndi iye.’​—Aroma 6:5. w20.12 5 ¶12; 6 ¶16-17

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Yohane 19:1-42

Lamlungu, April 17

Thupi limafesedwa lili lokhoza kuwonongeka, limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka.​—1 Akor. 15:42.

Mtumwi Paulo ankanena za munthu amene amaukitsidwa ndi “thupi lauzimu” lomwe lingathe kukakhala kumwamba. (1 Akor. 15:43, 44) Yesu ali padziko lapansili, anali ndi thupi lanyama koma ataukitsidwa anakhala “mzimu wopatsa moyo” ndipo anabwerera kumwamba. Mofanana ndi Yesu, Akhristu odzozedwa amaukitsidwa ndi matupi amene angathe kukakhala kumwamba. Paulo ananena kuti: “Monga tilili m’chifaniziro cha wopangidwa ndi fumbi uja, tidzakhalanso m’chifaniziro cha wakumwambayo.” (1 Akor. 15:45-49) Tiyenera kukumbukira kuti Yesu sanaukitsidwe ndi thupi lanyama. Paulo anafotokoza chifukwa chake. Iye anati: “Mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu” kumwamba. (1 Akor. 15:50) Atumwi komanso Akhristu odzozedwa saukitsidwa n’kupita kumwamba ndi matupi a nyama ndi magazi omwe angathe kuwola. w20.12 10-11 ¶10-12

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66 (Zochitika pa Nisani 16 dzuwa litalowa) Yohane 20:1

Lolemba, April 18

Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?​—1 Akor. 15:55.

M’nthawi ya atumwi, Mulungu anathandiza ophunzira ena a Yesu kuti alembe zokhudza anthu amene akuyembekezera kupita kumwamba. Mtumwi Yohane anafotokoza kuti: “Tsopano ndife ana a Mulungu, koma padakali pano sizinaonekerebe kuti tidzakhala otani. Tikudziwa kuti akadzaonekera, tidzakhala ngati iyeyo.” (1 Yoh. 3:2) Choncho Akhristu odzozedwa, sakudziwa kuti adzakhala otani akadzaukitsidwa kuti akakhale kumwamba ndi matupi auzimu. Komabe iwo akadzalandira mphoto yawo adzatha kumuona Yehova. Baibulo limatifotokozera zina zokhudza nkhani imeneyi. Odzozedwa adzakhala ndi Khristu akamadzathetsa “maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.” Zimenezi zikuphatikizaponso kuthetsa imfa “monga mdani womalizira.” Pamapeto pake Yesu adzaika zinthu zonse kuphatikizapo iyeyo ndi amene adzalamulire naye limodzi, pansi pa Yehova. (1 Akor. 15:24-28) Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. w20.12 8 ¶2

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Yohane 20:2-18

Lachiwiri, April 19

Ine ndili ndi chiyembekezo . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.​—Mac. 24:15.

Akhristu onse okhulupirika amene sakuyembekezera kupita kumwamba n’kukakhala ndi Khristu nawonso akuyembekezera kuti adzaukitsidwa. Baibulo limanena kuti mtumwi Paulo ndi ena opita kumwamba amaukitsidwa pa “kuuka koyambirira kuchokera kwa akufa.” (Afil. 3:11) Zimenezitu zikusonyeza kuti pambuyo pake padzakhalanso kuuka kwina. Ndipo izi n’zogwirizana ndi zomwe Yobu ankakhulupirira kuti zidzamuchitikira m’tsogolo. (Yobu 14:15) Ndiyeno “ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake” adzakhala ali ndi Yesu kumwamba pamene azidzathetsa maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. “Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” N’zoona kuti anthu amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba, sadzafanso. (1 Akor. 15:23-26) Zimene anthu amene adzakhale padziko lapansi akuyembekezera zikupezeka m’mawu a Paulo a mulemba la lero. N’zodziwikiratu kuti anthu osalungama sangapite kumwamba, choncho mawuwa akunena za kuukitsidwa kwa anthu padziko lapansi m’tsogolo. w20.12 6-7 ¶18-19

Lachitatu, April 20

[Khristu] anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.—Agal. 2:20.

Mwina tingamadzifunse kuti, ‘Kodi tingadziwe bwanji kuti Yehova amatikondabe ndipo angatikhululukire?’ Ngati mwafunsa funso limeneli ndi umboni wakuti Yehova angakukhululukireni. Zaka zambiri zapitazo Nsanja ya Olonda ina inafotokoza kuti: “Nthawi zina tingapezeke kuti tikuchita tchimo linalake mobwerezabwereza, zimenezi zingachitike chifukwa chakuti mwina sitinathetse vutolo tisanayambe kutumikira Mulungu. . . . Musaganize kuti mwachita tchimo limene Yehova sangakukhululukireni. Zimenezi ndi zimene Satana amafuna kuti muziganiza. Kukhumudwa kapena kudzimvera chisoni mukachita tchimo linalake ndi umboni wakuti si inu munthu woipa ndipo Yehova akhoza kukukhululukirani. Muyenera kukhala odzichepetsa n’kupitiriza kupemphera kuti Mulungu akukhululukireni, akuthandizeni kuti mukhalenso ndi chikumbumtima chabwino komanso akuthandizeni kuti musadzabwerezenso kuchita tchimolo.” Asanakhale Mkhristu, Mtumwi Paulo ankachita zinthu zambiri zoipa. Iye ankakumbukira zimene anachitazo. (1 Tim. 1:12-15) Komanso ankaona kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu anam’patsa iyeyo payekha. Choncho Paulo sankangodziimba mlandu, koma ankayesetsa kuchita zonse zimene angathe potumikira Yehova. w20.11 27 ¶14; 29 ¶17

Lachinayi, April 21

Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.​—Yak. 1:5.

Satana amagwiritsa ntchito zinthu zambiri pofuna kutiyesa kuti tichite zoipa. Ndiye kodi timatani zimenezi zikachitika? N’zosavuta kuganiza kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Mwachitsanzo, mwina tingaganize kuti: ‘Zinthuzi sizolakwika moti mpaka ndingachotsedwe nazo mumpingo.’ Kaganizidwe kameneka n’kolakwika kwambiri. Tingachite bwino kudzifunsa mafunso monga: ‘Kodi pamenepa Satana sakundiyesa kuti ndisiye kukhala ndi mtima wosagawanika? Ngati nditachita zinthu zoipazi, kodi sindinganyozetse dzina la Yehova? Kodi kuchita zimenezi kungandithandize kuti ndikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kapena ayi?’ Tiyenera kuganizira mafunso amenewa. Tizipempha Mulungu kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kuti tiyankhe mafunsowa moona mtima. Zimenezi zingatiteteze chifukwa zingatithandize kukana mayesero mwamphamvu ngati mmene Yesu anachitira. Paja iye nthawi ina ananena kuti: “Choka Satana!” (Mat. 4:10) Muzikumbukira kuti kukhala ndi mtima wogawanika n’kosathandiza. w20.06 12-13 ¶16-17

Lachisanu, April 22

Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.​—Aroma 12:3.

Timamvera Yehova modzichepetsa chifukwa timadziwa kuti iyeyo amadziwa zimene zingatithandize. (Aef. 4:22-24) Kudzichepetsa kumatithandiza kuona kuti kuchita chifuniro cha Yehova n’kofunika kwambiri kuposa zofuna zathu. Kumatithandizanso kuona kuti anthu ena amatiposa m’njira inayake. Zimenezi zingathandize kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso Akhristu anzathu. (Afil. 2:3) Ngati sitingasamale tikhoza kusokonezedwa ndi anthu a m’dziko la Satanali, omwe ndi onyada komanso odzikonda. Zikuoneka kuti Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi anatengera makhalidwe oipawa. Tikutero chifukwa mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu a ku Roma n’kuwauza kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.” Pamenepa Paulo anasonyeza kuti anthufe timafunikabe kudziganizira. Koma tiyenera kukhala odzichepetsa kuti tizidziona moyenera n’kupewa mtima wonyada. w20.07 2 ¶1-2

Loweruka, April 23

M’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse, komanso palibe anachita naye nkhondo.​—2 Mbiri 14:6.

Mu ulamuliro wa Asa, nthawi ya mtendere sinakhalepo mpaka kalekale. Gulu lalikulu la asilikali oposa 1 miliyoni linabwera kuchokera ku Itiyopiya. Mtsogoleri wa gululo, dzina lake Zera, ankaona kuti asilikali ake agonjetsa Yuda. Asa sankadalira kuchuluka kwa asilikali omwe anali nawo, koma ankadalira Mulungu wake Yehova. Iye anapemphera kuti: “Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu, ndipo tabwera m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli.” (2 Mbiri 14:11) Gulu la asilikali ochokera ku Itiyopiya linali lalikulu kuwirikiza kawiri kuposa gulu lankhondo la Asa. Komabe Asa ankadziwa kuti Yehova ndi wamphamvu ndipo akhoza kuthandiza anthu ake. Yehova sanagwiritse anthuwa fuwa la moto. Gulu lankhondo lochokera ku Itiyopiya lija linagonjetsedwa mochititsa manyazi. (2 Mbiri 14:8-13) Sitikudziwa kuti n’chiyani chomwe chidzatichitikire m’tsogolomu. Koma zimene tikudziwa n’zakuti mtendere umene anthu a Mulungu ali nawo panopa sudzakhalapo mpaka kalekale. Ndipotu Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza “mitundu yonse idzadana” ndi ophunzira ake.​—Mat. 24:9. w20.09 17-18 ¶14-16

Lamlungu, April 24

Ndimasangalala ndi . . . zitonzo.​—2 Akor. 12:10.

Palibe amene amasangalala akamanyozedwa. Koma ngati timakhumudwa kwambiri adani athu akamatinyoza, tikhoza kufooka. (Miy. 24:10) Ndiye kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani adani athu akamatinyoza? Mofanana ndi mtumwi Paulo, nafenso tikhoza kumasangalala anthu akamatinyoza. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti tikamanyozedwa komanso kuzunzidwa zimasonyeza kuti ndife otsatira enieni a Yesu. (1 Pet. 4:14) Yesu ananena kuti otsatira ake adzazunzidwa. (Yoh. 15:18-20) Zimenezi ndi zomwe zinachitikira Akhristu a munthawi ya atumwi. Pa nthawiyo, anthu amene ankatengera chikhalidwe cha Agiriki ankaona kuti Akhristu ndi anthu opanda nzeru komanso otsalira. Komanso Ayuda ankaona kuti Akhristu monga Petulo ndi Yohane anali anthu “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Akhristu ankaonedwa ngati anthu ofooka chifukwa sankachita nawo zandale kapena kumenya nkhondo moti anthu sankawalemekeza. Kodi Akhristu a munthawi ya atumwi analolera kusokonezedwa ndi maganizo a adani awowa? Ayi. w20.07 14-15 ¶3-4

Lolemba, April 25

Tiyeni tipitirize kukondana, chifukwa chikondi chimachokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu ndipo akudziwa Mulungu.​—1 Yoh. 4:7.

Mtumwi Yohane ankaganizira komanso kuwafunira zabwino abale ake. Zimenezi zimaonekera m’malangizo amene analemba m’makalata ake atatu ouziridwa. N’zosangalatsa kudziwa kuti nawonso amuna ndi akazi omwe adzalamulire ndi Yesu kumwamba ndi achikondi komanso oganizira ena ngati Yohane. (1 Yoh. 2:27) Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito malangizo amene anaperekawa. Tiyeni titsimikize mtima kuti tisasiye kuyenda m’choonadi pomvera Yehova pa zilizonse zomwe timachita. Nthawi zonse tiziphunzira Mawu ake n’kumawakhulupirira komanso tizikhulupirira Yesu. Tizipewa nzeru za anthu a m’dzikoli ndiponso ziphunzitso za anthu ampatuko. Tisamakhale moyo wachiphamaso komanso tisamakopeke ndi anthu amene angatinyengerere kuti tichite zoipa. Tizitsatira mfundo zabwino za Yehova. Komanso tiyeni tizithandiza abale athu kuti akhalebe olimba pokhululukira amene atilakwira komanso kuthandiza anthu amene ali pamavuto. Tikatero, tingapitirizebe kuyenda m’choonadi ngakhale zitakhala kuti tikukumana ndi mavuto. w20.07 24-25 ¶15-17

Lachiwiri, April 26

Mulungu anaika ziwalo m’thupi, chilichonse m’malo ake, mmene iye anafunira.​—1 Akor. 12:18.

Mwachikondi Yehova amapereka zochita zosiyanasiyana kwa atumiki ake okhulupirika mumpingo. Ngakhale zili choncho, tonsefe ndi amtengo wapatali ndipo timadalirana. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti mtumiki wa Yehova aliyense sayenera kumaona mnzake kuti ndi wosafunika, zomwe zingakhale ngati akumuuza kuti: “Ndilibe nawe ntchito.” (1 Akor. 12:21) Kuti mumpingo mukhale mtendere, tiyenera kumaona Akhristu anzathu kuti ndi ofunika n’kumagwira nawo ntchito limodzi. (Aef. 4:16) Tikamachita zinthu mogwirizana, zinthu zimayenda bwino mumpingo komanso timakondana kwambiri. Akulu onse mumpingo amaikidwa ndi mzimu wa Yehova. Komabe, aliyense amakhala ndi mphatso komanso luso losiyana ndi la mnzake. (1 Akor. 12:17) Akulu amene atumikira kwa nthawi yaitali angakhale kuti akudziwa zambiri kusiyana ndi amene angoikidwa kumene. Ena sangakwanitse kuchita zambiri chifukwa ndi achikulire kapena amadwaladwala. Koma ngakhale zili choncho, palibe mkulu amene ayenera kumaona anzake kuti ndi osafunika, zomwe zingakhale ngati akuwauza kuti: “Ndilibe nanu ntchito.” M’malomwake, mkulu aliyense ayenera kutsatira malangizo amene Paulo analemba pa Aroma 12:10. w20.08 26 ¶1-2; 27 ¶4

Lachitatu, April 27

Zochitika za padzikoli zikusintha.​—1 Akor. 7:31.

Yehova amatitsogolera panjira yopita ku moyo pogwiritsa ntchito mbali yapadziko lapansi ya gulu lake. Mosakayikira gulu la Yehova likatifotokozera kuti pali kusintha pa mfundo zina za m’Baibulo zimene timakhulupirira poyamba kapena malangizo okhudza makhalidwe, timavomereza ndipo timatsatira. Koma kodi timatani gulu la Yehova likasintha zinthu zina zimene zikukhudza moyo wathu, ngati kugulitsidwa kwa Nyumba ya Ufumu imene ifeyo timasonkhanamo? Tidzakhalabe osangalala tikamakumbukira kuti ntchito yomwe tikugwirayi ndi ya Yehova komanso kuti ndi amene akutsogolera gulu lake. (Akol. 3:23, 24) Mfumu Davide anapereka chitsanzo chabwino pamene ankapereka ndalama zomangira kachisi. Iye anati: “Ndine ndani ine, ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupereka nsembe zaufulu ngati zimenezi? Pakuti chilichonse n’chochokera kwa inu, ndipo tapereka kwa inu zochokera m’dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Tikamapereka zopereka ifenso timakhala tikum’patsa Yehova zinthu zimene watipatsa. Komabe iye amayamikira kwambiri tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso ndalama zathu pothandizira pa ntchito yake.​—2 Akor. 9:7. w20.11 22-23 ¶14-16

Lachinayi, April 28

Woyang’ana mitambo sadzakolola.​—Mlal. 11:4.

Amboni za Yehovafe sitiona kuti zinthu zikutiyendera bwino potengera kuchuluka kwa anthu omwe tawathandiza kuti alowe m’gulu la Mulungu. (Luka 8:11-15) Tikamapitiriza kulalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa ena, Yehova amaona kuti zinthu zikutiyendera bwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa timakhala tikumumvera komanso tikumvera Mwana wake. (Maliko 13:10; Mac. 5:28, 29) Tikufunika kulimbikira kugwira ntchito yolalikira panopa. Tikutero chifukwa mapeto a dzikoli akuyandikira. Kwatsala kanthawi kochepa kuti tigwire ntchito yolalikirayi, yomwe ingapulumutse anthu. Choncho musamadikire kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino pa moyo wanu kuti muyambe kugwira nawo ntchito yofunikayi. Muyenera kuyesetsa panopa kuti muzikonda kwambiri ntchito yolalikira, muzidziwa bwino mfundo za m’Baibulo, muzigwira ntchito yolalikira molimba mtima komanso muzikhala opirira. Mukatero mudzakhala m’gulu la anthu oposa 8 miliyoni amene amalalikira uthenga wabwino padziko lonse ndipo mudzakhala ndi chimwemwe chimene Yehova amapereka. (Neh. 8:10; Luka 5:10) Muzilalikira mmene mungathere mpaka pamene Yehova adzanene kuti ntchitoyi yafika kumapeto. w20.09 7 ¶18-20

Lachisanu, April 29

Sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako.​—1 Tim. 6:20.

Tiyenera kupewa kulakalaka chuma. Tikutero chifukwa “chinyengo champhamvu cha chuma” chingatichititse kusiya kukonda Yehova, kuyamikira Mawu ake komanso kuuza ena Mawu akewo. (Mat. 13:22) Kuti titeteze zinthu zimene Yehova watipatsa tiyenera kuchita zinthu mwamsanga tikaona zinthu zimene zingatisokoneze pomutumikira. Tiyenera kuoneratu khomo lotulukira ngati mwadzidzidzi pogwiritsa ntchito intaneti, poonera filimu kapena poonera pulogalamu ya pa TV taona zinthu zolaula, zachiwawa kapena nkhani za ampatuko. Tikadziwiratu zoyenera kuchita ngati zoterezi zitachitika, tingathe kuchita zinthu mwamsanga poteteza ubwenzi wathu ndi Yehova kuti tikhalebe oyera pamaso pake. (Sal. 101:3; 1 Tim. 4:12) Tiyenera kuteteza zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa zomwe ndi choonadi cha m’Baibulo komanso kuphunzitsa ena. Tikamachita zimenezi, tidzakhala ndi chikumbumtima choyera, moyo watanthauzo komanso tidzakhala osangalala chifukwa chothandiza ena kudziwa Yehova. w20.09 30 ¶16-19

Loweruka, April 30

Maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.​—Yes. 30:20.

Kodi ndinu obatizidwa? Ngati ndi choncho munasonyeza poyera kuti mumakhulupirira Yehova komanso kuti mukufunitsitsa kumutumikira limodzi ndi gulu lake. Masiku ano Yehova amatsogolera gulu lake m’njira imene imasonyeza makhalidwe ake, cholinga chake komanso mfundo zake. Taonani makhalidwe atatu a Yehova amene timawaona m’gulu lake. Choyamba, “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34) Chikondi ndi chimene chinapangitsa Yehova kuti apereke Mwana wake kuti akhale “dipo . . . m’malo mwa onse.” (1 Tim. 2:6; Yoh. 3:16) Yehova amagwiritsa ntchito anthu ake polalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene angamvetsere. Zimenezi zimathandiza anthu ambiri kuti apindule ndi dipo la Yesu n’kudzapulumuka. Chachiwiri, Yehova ndi Mulungu wadongosolo komanso wamtendere. (1 Akor. 14:33, 40) Choncho tingayembekezere kuti anthu amene amamutumikira azimutumikira mwadongosolo komanso mwamtendere. Chachitatu, Yehova ndi “Mlangizi Wamkulu.” (Yes. 30:21) N’chifukwa chake gulu lake limayesetsa kuphunzitsa Mawu ake mumpingo komanso mu utumiki. w20.10 20 ¶1-3

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena