May
Lamlungu, May 1
Anapitiriza kuwamvera.—Luka 2:51.
Yesu ali mwana, anasankha kuti azimvera makolo ake. Iye sanakane kumvera makolo ake poganiza kuti ankadziwa zinthu zambiri kuposa iwowo. Yesu anali ndi udindo waukulu chifukwa anali mwana woyamba ndipo ankayesetsa kukwaniritsa udindo wakewo. Iye anayesetsa kuphunzira ntchito ya ukalipentala kuchokera kwa Yosefe bambo ake, n’cholinga choti azipeza ndalama zothandizira banja lawo. Makolo ake a Yesu ayenera kuti anamufotokozera zodabwitsa zimene zinachitika kuti abadwe komanso zimene angelo ananena zokhudza iyeyo. (Luka 2:8-19, 25-38) Komabe Yesu sankangodalira zimene makolo ake ankamuuza koma nayenso ankaphunzira Malemba payekha. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama? Tikudziwa zimenezi chifukwa iye ali mnyamata, aphunzitsi ku Yerusalemu “anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:46, 47) Ndipo ali ndi zaka 12 zokha, Yesu anali atasonyeza kale kuti Yehova ndi Atate ake.—Luka 2:42, 43, 49. w20.10 29-30 ¶13-14
Lolemba, May 2
Khristu anaukitsidwa kwa akufa.—1 Akor. 15:12.
Kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa n’kumene kumatithandiza kuti tizikhulupirira kuti anthu enanso adzaukitsidwa. Paulo atangoyamba kulemba zokhudza kuuka kwa akufa, anatchula mfundo zitatu izi: (1) “Khristu anafera machimo athu.” (2) “Anaikidwa m’manda.” (3) “Anaukitsidwa tsiku lachitatu, mogwirizana ndi Malemba. (1 Akor. 15:3, 4) Kodi imfa, kuikidwa m’manda komanso kuukitsidwa kwa Yesu zili ndi tanthauzo lotani kwa ife? Mneneri Yesaya ananeneratu kuti Mesiya ‘adzadulidwa m’dziko la amoyo’ ndipo “manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa.” Koma panalinso zina zimene zinkayenera kuchitika. Iye ananenanso kuti Mesiya adzanyamula “tchimo la anthu ambiri.” Yesu anachita zimenezi pamene anapereka moyo wake monga dipo. (Yes. 53:8, 9, 12; Mat. 20:28; Aroma 5:8) Choncho imfa, kuikidwa m’manda ndiponso kuukitsidwa kwa Yesu zimatipatsa zifukwa zamphamvu zokhulupirira kuti tidzamasulidwa ku uchimo ndi imfa komanso kuti tidzaonananso ndi achibale athu omwe anamwalira. w20.12 2-3 ¶4-6; 5 ¶11
Lachiwiri, May 3
Ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika. Ngati alipo munthu woganiza kuti ali ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndiye woposa ameneyo.—Afil. 3:4.
Mtumwi Paulo ankakonda kulalikira m’masunagoge a Chiyuda. Mwachitsanzo, musunagoge wa ku Tesalonika, “kwa masabata atatu anakambirana nawo [Ayuda] mfundo za m’Malemba.” (Mac. 17:1, 2) Paulo ayenera kuti ankamasuka kukambirana ndi anthu musunagoge chifukwa anakulira m’chipembedzo cha Chiyuda. (Mac. 26:4, 5) Iye ankamvetsa bwino Ayuda choncho ankatha kuwalalikira mopanda mantha. (Afil. 3:4, 5) Paulo atathamangitsidwa ndi adani ku Tesalonika komanso ku Bereya, anafika ku Atene. Kumeneko anapitanso musunagoge ndipo ‘anayamba kukambirana ndi Ayuda komanso anthu ena opembedza Mulungu.’ (Mac. 17:17) Koma mumsika anapeza anthu osiyana kwambiri ndi Ayuda. Pa anthu amene ankawalalikira kumeneko panali akatswiri a nzeru za anthu komanso anthu amitundu ina omwe ankaona kuti uthenga wa Paulo unali ‘chiphunzitso chatsopano.’ Iwo anamuuza kuti: “Zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo m’makutu mwathu.”—Mac. 17:18-20. w20.04 9 ¶5-6
Lachitatu, May 4
Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.—Aroma 7:21.
Ngati mukuvutika kuti musiye khalidwe linalake loipa musadzione ngati wachabechabe. Popeza kuti tonsefe timalakwitsa zinthu timafuna kuti Yehova azitisonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, ndipo zimenezi zimatheka chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Aef. 1:7; 1 Yoh. 4:10) Komanso abale ndi alongo athu mumpingo angatilimbikitse. Iwo angamvetsere pamene tikuwafotokozera mavuto athu. (Miy. 12:25; 1 Ates. 5:14) Mlongo wina wa ku Nigeria dzina lake Joy amene wakhala akulimbana ndi zinthu zina zimene zinkamufooketsa ananena kuti: “Sindikanatha kupirira zikanakhala kuti abale ndi alongo sanandithandize. Zimene iwo ankachita pondilimbikitsa ndi umboni wakuti Yehova amayankha mapemphero anga. Abale ndi alongowa andiphunzitsanso mmene ndingalimbikitsire anthu ena amene ali pa mavuto.” Komabe tizikumbukira kuti si nthawi zonse pamene abale ndi alongo athu angadziwe kuti tikufunika kulimbikitsidwa. Choncho tingafunike kupita kwa m’bale kapena mlongo wolimba mwauzimu n’kumufotokozera mavuto athu. w20.12 23-24 ¶7-8
Lachinayi, May 5
Ndakutchani mabwenzi.—Yoh. 15:15.
Kuti tiyambe kugwirizana ndi munthu wina, nthawi zambiri timafunika kupeza nthawi yocheza naye. Zili choncho chifukwa mumauzana maganizo komanso zimene zakuchitikirani pa moyo wanu. Koma si zophweka kuti Yesu akhale mnzathu wapamtima. Kodi chimene chimachititsa kuti zikhale zovuta n’chiyani? Vuto loyamba ndi lakuti ifeyo sitinakumanepo ndi Yesu. Akhristu ena mu nthawi ya atumwi analinso ndi vuto lomweli. Koma mtumwi Petulo anawauza kuti: “Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye.” (1 Pet. 1:8) Choncho ndi zotheka kukhala anzake a Yesu ngakhale kuti sitinakumanepo naye. Vuto lachiwiri ndi loti sitingalankhule ndi Yesu. Tikamapemphera timalankhula ndi Yehova. N’zoona kuti timapemphera m’dzina la Yesu, koma sitilankhula ndi Yesuyo. Ndipo Yesu safuna kuti tizipemphera kwa iye. Zili choncho chifukwa chakuti pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu, ndipo Yehova yekha ndi amene tiyenera kumulambira. (Mat. 4:10) Komabe tikhoza kusonyeza kuti timakonda Yesu. w20.04 20 ¶1-3
Lachisanu, May 6
[Mulungu] adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.—1 Pet. 5:10.
Anthu othamanga pa mpikisano ku Girisi ankatopa komanso kumva kupweteka. Zimene ankadalira kuti apirire mavutowo zinali mphamvu zawo komanso zimene anaphunzira pokonzekera mpikisano basi. Nafenso timaphunzira mmene tingathamangire pa mpikisano wokalandira moyo. Koma tili ndi zinthu zinanso zimene zimatithandiza. Timadalira Yehova yemwe ali ndi mphamvu zopanda malire. Komanso iye analonjeza kuti azitiphunzitsa komanso kutilimbitsa. Mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ankanyozedwa, kuzunzidwa, kutopa komanso kupirira vuto lina limene analitchula kuti “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Iye sankaona kuti zimenezi ndi zifukwa zomuchititsa kusiya kutumikira Yehova koma ankaona kuti ndi mwayi woti azimudalira. (2 Akor. 12:9, 10) Popeza Paulo anali ndi maganizo amenewa, Yehova anamuthandiza pa mavuto ake onse. w20.04 29 ¶13-14
Loweruka, May 7
Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate.—Yoh. 6:44.
Tilinso ndi mphatso ina yamtengo wapatali yosaoneka yomwe ndi ‘kugwira ntchito limodzi’ ndi Yehova, Yesu komanso angelo. (2 Akor. 6:1) Timagwira nawo ntchito pamene tikulalikira komanso kuphunzitsa anthu. Paulo ananena za anthu onse amene amagwira ntchitoyi kuphatikizapo iyeyo kuti: “Ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Tikamagwira ntchito yolalikirayi timakhalanso antchito anzake a Yesu. Paja iye atauza otsatira ake kuti ‘akaphunzitse anthu a mitundu yonse,’ ananenanso kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mat. 28:19, 20) Nanga bwanji za angelo? Ndi mwayi waukulu kutsogoleredwa ndi angelo tikamalalikira “uthenga wabwino wosatha . . . kwa anthu okhala padziko lapansi.” (Chiv. 14:6) Kodi takwanitsa kuchita chiyani chifukwa chothandizidwa ndi Yehova, Yesu, komanso angelo? Tikamafesa mbewu za uthenga wa Ufumu, zina zimagwera m’mitima ya anthu omvetsera ndipo zimakula. (Mat. 13:18, 23) Koma kodi ndi ndani amene amachititsa kuti mbewu za choonadi zikule ndi kubereka zipatso? Yesu anafotokoza yankho la funso limeneli mulemba la leroli. w20.05 30 ¶14-15
Lamlungu, May 8
Musamatengere nzeru za nthawi ino.—Aroma 12:2.
Masiku ano, anthu ambiri amathetsa mabanja awo. Ngakhale anthu a banja limodzi omwe akukhala nyumba imodzi, nthawi zina akhoza kumaonana ngati alendo. Mlangizi wina wa mabanja ananena kuti: “M’mabanja ambiri amayi, abambo ndi ana sachitira zinthu limodzi. Iwo amathera nthawi yambiri pa kompyuta, tabuleti, foni kapenanso masewera a pakompyuta.” Choncho ngakhale kuti amakhala nyumba imodzi, anthuwa sadziwana bwino. Ife sitikufuna kukhala ngati anthu a m’dzikoli omwe alibe chikondi. M’malomwake, tiyenera kusonyeza chikondi chenicheni osati kwa achibale athu okha, koma tiyenera kumasonyezanso chikondichi kwa abale ndi alongo athu mumpingo. (Aroma 12:10) Kodi mawu akuti chikondi chenicheni amatanthauza chiyani? Mawu amenewa amanena za kugwirizana komwe kumakhalapo pakati pa anthu a banja limodzi. Chimenechi ndi chikondi chimene tiyenera kusonyezanso kwa abale ndi alongo athu mumpingo. Tikamasonyeza chikondi chenicheni zimathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana ndipo timatumikira Yehova limodzi mosangalala.—Mika 2:12. w21.01 20 ¶1-2
Lolemba, May 9
Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.—Sal. 86:11.
Timu yomwe osewera ake ndi ogwirizana ingakhale ndi mwayi waukulu wopambana kusiyana ndi timu imene osewera ake sagwirizana. Mtima wanu ungafanane ndi timu imene ingapambaneyi ngati zimene mumaganiza, kulakalaka komanso mmene mumamvera n’zogwirizana ndi kutumikira Yehova. Musaiwale kuti Satana amafuna mukhale ndi mtima wogawanika. Iye amafuna kuti zimene mumaganiza, kulakalaka komanso mmene mumamvera zizisemphana ndi mfundo za Yehova. Koma kuti muzitumikira Yehova, mumafunika kuti mukhale ndi mtima wosagawanika. (Mat. 22:36-38) Choncho musalole kuti Satana akuchititseni kukhala ndi mtima wogawanika. Tizipemphera kwa Yehova ngati mmene anachitira Davide kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” Ndiyeno tiziyesetsa mmene tingathere kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lathulo. Tsiku lililonse tiziyesetsa kuti zosankha zathu zonse zizisonyeza kuti timaopa dzina loyera la Yehova. Monga Mboni zake, tikamachita zimenezi tingathandize kuti ena azilemekeza dzina lake. (Miy. 27:11) Ndipotu tingalankhule ngati mneneri Mika yemwe ananena kuti: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5. w20.06 13 ¶17-18
Lachiwiri, May 10
Iyo idzapita ndi ukali waukulu kuti ikafafanize ndi kuwononga ambiri.—Dan. 11:44.
Mfumu ya kumpoto limodzi ndi maboma onse a padziko lapansi akadzaukira anthu a Mulungu, Mulungu Wamphamvuyonse adzakwiya kwambiri ndipo nkhondo ya Aramagedo idzayamba. (Chiv. 16:14, 16) Pa nthawiyi, mfumu ya kumpoto ndi mayiko onse amene apanga Gogi wa ku Magogi, adzawonongedwa ndipo ‘sipadzapezeka wowathandiza.’ (Dan. 11:45) Vesi lotsatira mu ulosi wa Danieli limafotokoza za mmene mfumu ya kumpoto ndi mayiko ogwirizana nalo adzawonongedwere komanso mmene tidzapulumukire. (Dan. 12:1.) Kodi vesili likutanthauza chiyani? Mikayeli ndi dzina lina la Mfumu yathu Khristu Yesu. Iye wakhala ‘ataimirira’ kuti athandize anthu a Mulungu kuyambira mu 1914 pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba. Posachedwapa iye “adzaimirira” kapena kuti adzawononga adani ake pankhondo ya Aramagedo. Nkhondo imeneyi idzakhala chinthu chomaliza pa zomwe zidzachitike pa nthawi yomwe Danieli anaitchula kuti ndi “nthawi ya masautso” aakulu amene sanachitikepo. Ulosi wa Yohane wopezeka m’buku la Chivumbulutso umatchula nthawi imeneyi kuti “chisautso chachikulu.”—Chiv. 6:2; 7:14. w20.05 15-16 ¶15-17
Lachitatu, May 11
Yosefe . . . anapita naye ku Iguputo.—Gen. 39:1.
Pamene Yosefe anali kapolo komanso pamene anali m’ndende, sakanatha kuchita chilichonse kuti asinthe mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Ndiye kodi n’chiyani chimene chinamuthandiza kuti aziona zinthu moyenera? M’malo momangoganizira zinthu zimene sakanatha kuchita, ankadzipereka kwambiri kugwira ntchito iliyonse imene wapatsidwa. Yosefe nthawi zonse ankaona kuti Yehova ndi wofunika kwambiri pa moyo wake. Chifukwa cha zimenezi, Yehova anadalitsa chilichonse chimene Yosefe ankachita. (Gen. 39:21-23) Nkhani ya Yosefe imatikumbutsa kuti anthu m’dzikoli ndi ankhanza ndipo angatichitire zinthu zopanda chilungamo. Ngakhale abale ndi alongo akhoza kutichitira zinthu zimene zingatikhumudwitse. Koma tikamaona Yehova ngati thanthwe lathu kapena malo athu othawirapo, sitingataye mtima kapena kusiya kumutumikira. (Sal. 62:6, 7; 1 Pet. 5:10) Tizikumbukiranso kuti Yosefe anali ndi zaka 17 pamene Yehova anamulotetsa maloto ake aja. Choncho zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amadaliranso atumiki ake achinyamata. Masiku ano pali achinyamata ambiri amene ali ngati Yosefe, nawonso amakhulupirira kwambiri Yehova. Ena mwa achinyamata amenewa afika mpaka pomangidwa chifukwa sanafune kusiya kukhala okhulupirika kwa Mulungu.—Sal. 110:3. w20.12 16 ¶3; 17 ¶5, 7
Lachinayi, May 12
Anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu.—Mac. 5:40.
Mtumwi Petulo ndi mtumwi Yohane ankaona kuti ndi mwayi kuzunzidwa chifukwa chotsatira Yesu komanso kuuza ena zimene Yesu ankaphunzitsa. (Mac. 4:18-21; 5:27-29, 41,42) Otsatira a Yesu sankachita manyazi. Ngakhale kuti anthu a m’madera amene ankakhala sankawalemekeza, Akhristuwa anathandiza anthu ambiri kuposa adani awowo. Mwachitsanzo, mabuku a m’Baibulo omwe ena mwa Akhristuwa analemba anathandiza anthu ambirimbiri komanso kuwapatsa chiyembekezo. Ufumu umene ankalalikira unayamba kulamulira kumwamba ndipo posachedwapa uyamba kulamulira dziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Mosiyana ndi zimenezi, ulamuliro wa Roma womwe unkazunza Akhristu pa nthawiyo, unatha. Komanso panopo Akhristu okhulupirikawo akulamulira monga mafumu kumwamba. Adani amene ankawatsutsawo anamwalira ndipo ngati angadzaukitsidwe, azidzalamuliridwa ndi Ufumu umene Akhristu omwe ankadana nawowo ankalalikira.—Chiv. 5:10. w20.07 15 ¶4
Lachisanu, May 13
[Abulahamu] anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.—Aheb. 11:10.
Abulahamu ankakhulupirira kwambiri zimene Mulungu anamulonjeza moti ankatha kuona Wodzozedwayo, kapena kuti Mesiya, yemwe anadzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. N’chifukwa chake Yesu anauza Ayuda kuti: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa, ndipo analiona moti anakondwera.” (Yoh. 8:56) N’zoonekeratu kuti Abulahamu ankadziwa kuti ena mwa ana ake adzakhala mafumu mu Ufumu umene Mulungu adzakhazikitse ndipo ankayembekezera kuti Yehova adzakwaniritse zimene anamulonjeza. Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankayembekezera “mzinda” kapena Ufumu wokhazikitsidwa ndi Mulungu? Iye sanakhale nzika ya ufumu uliwonse wapadziko lapansi komanso ankakhala moyo woyendayenda ndipo sanali mbali ya ufumu uliwonse. Kuwonjezera apo, Abulahamu sanayese kukhazikitsa ufumu wake. M’malomwake anapitiriza kumvera Yehova kwinaku akuyembekezera kuti adzakwaniritse zomwe anamulonjeza. Zimene anachitazi zinasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. w20.08 3 ¶4-5
Loweruka, May 14
Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.—Aroma 6:7.
Yehova analonjeza kuti mu ulamuliro wa Khristu, palibe amene adzanene kuti: “Ndikudwala.” (Yes. 33:24) Choncho Yehova akamadzaukitsa anthuwa adzawalengera matupi athanzi. Koma si kuti iwo adzangofikira kukhala angwiro. Zitakhala choncho, ndiye kuti achibale komanso anzawo sangadzawazindikire. Zikuoneka kuti anthu onse azidzasintha pang’onopang’ono mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, mpaka kukhala angwiro. Ndipo pamapeto pa zaka 1,000 zimenezi, Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake. Pa nthawiyi Ufumuwu udzakhala utakwaniritsa cholinga chake kuphatikizapo kuthandiza anthu onse kuti akhale angwiro. (1 Akor. 15:24-28; Chiv. 20:1-3) Taganizirani mmene mudzasangalalire kulandiranso achibale ndi anzanu amene anamwalira. Mwina muzidzangosekerera kapenanso kugwetsa misozi yachisangalalo. N’kuthekanso kuti muzidzayimba nyimbo zotamanda Yehova. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zidzakuthandizani kukonda kwambiri Atate wanu wachikondi komanso Mwana wake, omwe adzaukitse anthu amene anamwalira. w20.08 16-17 ¶9-10
Lamlungu, May 15
Aliyense ali ndi mphatso yake yochokera kwa Mulungu, wina m’njira iyi, winanso m’njira inayo.—1 Akor. 7:7.
Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuganizira ngati angathe kutumikira Yehova asali pabanja. (1 Akor. 7:8, 9) Mwachionekere, Paulo sankaona Akhristu omwe sali pabanja ngati otsika. N’chifukwa chake iye anasankha Timoteyo, yemwe anali wosakwatira, kuti azisamalira maudindo aakulu m’gulu la Yehova. (Afil. 2:19-22) Choncho, zingakhale zolakwika kuganiza kuti m’bale ndi woyenerera potengera kuti ndi wokwatira kapena ndi wosakwatira. (1 Akor. 7:32-35, 38) Yesu kapena Paulo sanaphunzitse kuti Akhristu ayenera kukhala pabanja kapena ayi. Ndiye tinganene zotani pa nkhani ya kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja? Nsanja ya Olonda ya October 1, 2012 inapereka yankho labwino la funsoli. Inati: “Kunena zoona, zonsezi [kukhala pabanja komanso kusakhala pabanja] ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. . . . Yehova saona kuti kusakhala pabanja ndi chinthu chochititsa manyazi kapena chomvetsa chisoni.” Choncho, tiyenera kulemekeza abale ndi alongo amumpingo mwathu omwe sali pabanja. w20.08 28 ¶8-9
Lolemba, May 16
Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, . . . koma Atate yekha.—Mat. 24:36.
M’mayiko ena, anthu amafuna kuphunzira zambiri akamva uthenga wabwino moti amasangalala kwambiri ndi uthengawo. Pomwe m’mayiko ena, anthu sachita chidwi ndi nkhani za Mulungu kapena Baibulo. Kodi anthu a m’dera lanu amatani akamva uthenga wabwino? Kaya amachita zotani, Yehova amafuna tipitirizebe kulalikira mpaka ntchitoyi itafika kumapeto. Yehova anaikiratu nthawi yomwe tidzasiye kugwira ntchito yolalikira, “ndipo kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Yesu anauza ophunzira ake zokhudza makhalidwe a anthu komanso zimene zidzachitike m’masiku otsiriza. Iye ankadziwa kuti zinthu zimenezi zingachititse otsatira ake kusiya kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Choncho anauza ophunzira ake kuti “khalanibe maso.” (Mat. 24:42) Mu nthawi ya Nowa, panali zinthu zambiri zimene zinkachititsa anthu kuti azinyalanyaza uthenga umene ankawauza. Zangati zimenezi zingachitikenso masiku ano. (Mat. 24:37-39; 2 Pet. 2:5) Choncho tiyenera kuyesetsa kuti tipitirizebe kuona ntchito imene Yehova anatipatsa kukhala yofunika kwambiri. w20.09 8 ¶1-2, 4
Lachiwiri, May 17
Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.—2 Tim. 3:12.
Satana “ali ndi mkwiyo waukulu” ndipo kungakhale kudzinamiza kuganiza kuti tingamangoyenda moyera. (Chiv. 12:12) Posachedwapa tonse tikumana ndi mayesero aakulu. Padzikoli padzachitika “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano.” (Mat. 24:21) Pa nthawiyo, achibale athu akhoza kudzatiukira ndipo ntchito yathu ikhoza kudzaletsedwa. (Mat. 10:35, 36) Kodi pa nthawiyo aliyense wa ife azidzadalira Yehova kuti amuthandize ndi kumuteteza ngati mmene Mfumu Asa anachitira? (2 Mbiri 14:11) Yehova wakhala akutithandiza kukonzekera zinthu zimene zikubwera kutsogoloku. Iye akutsogolera “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa “chakudya pa nthawi yoyenera” kuti tikhale olimba mwauzimu. (Mat. 24:45) Koma aliyense wa ife ayenera kuyesetsa kuti azikhulupirira kwambiri Yehova.—Aheb. 10:38, 39. w20.09 18 ¶16-18
Lachitatu, May 18
Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova. Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.—Miy. 21:1.
Yehova akhoza kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu kwambiri, kuchititsa anthu amene ali ndi udindo kuti achite zimene iyeyo akufuna ngati zinthuzo n’zogwirizana ndi chifuniro chake. Anthu angakumbe ngalande kuti apatutse madzi a mumtsinje n’cholinga chakuti azipita kumene iwowo akufuna. Mofanana ndi zimenezi Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake posintha maganizo a olamulira kuti achite zinthu zimene zingakwaniritse cholinga chake. Zikatero anthu olamulira amatha kusankha zinthu zimene zingathandize anthu a Mulungu. (Yerekezerani ndi Ezara 7:21, 25, 26.) Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani? Tingathe kupempherera ‘mafumu ndi anthu onse apamwamba,’ pamene akusankha zinthu zimene zingakhudze kulambira kwathu. (1 Tim. 2:1, 2; Neh. 1:11) Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, ifenso timapempherera mosalekeza abale ndi alongo athu amene ali m’ndende.—Mac. 12:5; Aheb. 13:3. w20.11 15 ¶13-14
Lachinayi, May 19
Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.—Mat. 28:19.
Mumasangalala kwambiri kuona munthu amene mumaphunzira naye Baibulo akubatizidwa. (1 Ates. 2:19, 20) Ophunzira Baibulo amene angobatizidwa kumene amakhala ngati ‘makalata ochitira umboni,’ osati kwa anthu amene amaphunzira nawo okha komanso kwa mpingo wonse. (2 Akor. 3:1-3) N’zosangalatsa kuona kuti m’zaka 4 zapitazi, mwezi uliwonse timachititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 10,000,000 padziko lonse ndipo m’zaka zimenezi anthu oposa 280,000 ankabatizidwa chaka chilichonse kukhala a Mboni za Yehova komanso ophunzira a Yesu Khristu. Ndiye kodi tingatani kuti tithandize anthu mamiliyoni amenewa omwe timaphunzira nawo Baibulo kuti abatizidwe? Yehova moleza mtima akuperekabe mwayi kwa anthu kuti akhale ophunzira a Khristu. Panopa nthawi yatha, choncho tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tithandize anthu amenewa kuti abatizidwe mwamsanga.—1 Akor. 7:29a; 1 Pet. 4:7. w20.10 6 ¶1-2
Lachisanu, May 20
Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.
Mfumu Sauli sanamvere Yehova. Ndipo pamene mneneri Samueli ankamufunsa za nkhaniyi, Sauli anakana kuvomereza zimene analakwitsa. M’malomwake, iye anayesa kudziikira kumbuyo ponena kuti sinali nkhani yaikulu komanso ananena kuti anthu ena ndi omwe anamukakamiza kuchita zimene anachitazo. (1 Sam. 15:13-24) M’mbuyomu, Sauli anali atachitanso zofanana ndi zimenezi. (1 Sam. 13:10-14) N’zomvetsa chisoni kuti anayamba kukhala ndi mtima wodzikuza. Iye sanasinthe maganizo ake ndipo Yehova anamudzudzula komanso anamukana. Palibe amene angafune kukhala ngati Sauli. Choncho tingachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Ndikawerenga malangizo a m’Mawu a Mulungu, kodi ndimadziikira kumbuyo kapena kupeza zifukwa zondichititsa kuti ndisatsatire malangizowo? Kodi ndimaganiza kuti zimene ndikuchita si zoipa kwenikweni? Kodi ndimaimba ena mlandu chifukwa cha zimene ndikuchita?’ Ngati yankho ndi loti inde pa lililonse la mafunsowa, ndiye kuti tiyenera kusintha maganizo athu. Ngati sitingatero, tingayambe kukhala ndi mtima wodzikuza ndipo Yehova angatikane kuti tisakhalenso anzake. w20.11 20 ¶4-5
Loweruka, May 21
Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako, asanafike masiku oipa komanso zisanafike zaka zimene udzati: “Moyo sukundisangalatsa.”—Mlal. 12:1.
Achinyamata, musankhe amene mukufuna kumutumikira. Muyenera kumudziwa bwino Yehova, zimene amafuna komanso mmene mungachitire zimene amafunazo pa moyo wanu. (Aroma 12:2) Mukatero ndi pamene mungathe kusankha kutumikira Yehova, chomwe ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu. (Yos. 24:15; Mlal. 12:1) Mukamawerenga komanso kuphunzira Baibulo nthawi zonse, mudzapitiriza kukonda kwambiri Yehova komanso chikhulupiriro chanu chidzalimba. Sankhani kuti zimene Yehova amafuna zikhale pamalo oyamba m’moyo wanu. Dziko la Satanali limalonjeza kuti achinyamata akamagwiritsa ntchito luso lawo pochita zinthu zodzipindulitsa okha angakhale osangalala. Koma zoona n’zakuti anthu amene amangokhalira kufunafuna chuma amadzibweretsera “zopweteka zambiri pathupi lawo.” (1 Tim. 6:9, 10) Komabe mukamvera Yehova komanso kusankha kuti zimene amafuna zikhale pamalo oyamba m’moyo wanu, zinthu zidzakuyenderani bwino ndipo ‘mudzachita zinthu mwanzeru.’—Yos. 1:8. w20.10 30-31 ¶17-18
Lamlungu, May 22
Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu . . . , chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.—Luka 4:43.
Munthawi ya atumwi, uthenga umene Yesu ankalalikira unkapereka chiyembekezo kwa anthu onse. Iye analamula otsatira ake kuti apitirize kugwira ntchito imene anayambitsa yochitira umboni “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) N’zoona kuti iwo sakanakwanitsa kugwira ntchito imeneyi ndi mphamvu zawo zokha. Ankafunika mzimu woyera kapena kuti “mthandizi” amene Yesu anawalonjeza. (Yoh. 14:26; Zek. 4:6) Otsatira a Yesu analandira mzimu woyera pa Pentekosite mu 33 C.E. Mzimuwo unawathandiza ndipo nthawi yomweyo anayamba kugwira ntchito yolalikira. M’kanthawi kochepa anthu ambiri anamva uthenga wabwino. (Mac. 2:41; 4:4) Pamene anthu anayamba kuwazunza, ophunzirawo sanachite mantha n’kusiya kulalikira, m’malomwake anapempha Mulungu kuti awathandize. Iwo anapemphera kuti: “Lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Kenako iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo “anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.”—Mac. 4:18-20, 29, 31. w20.10 21 ¶4-5
Lolemba, May 23
Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba . . . ndiponso anaukitsidwa.—1 Akor. 15:3, 4.
N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yehova anaukitsa Yesu? Panali anthu ambiri amene anaona Yesu ataukitsidwa ndipo anafotokozera ena zimenezi. (1 Akor. 15:5-7) Munthu woyamba amene mtumwi Paulo anatchula kuti anaona Yesu ataukitsidwa anali mtumwi Petulo (Kefa). Ophunzira enanso anatsimikizira kuti Petulo anaona Yesu ataukitsidwa. (Luka 24:33, 34) Kuwonjezera pamenepo, Paulo ananena kuti atumwi 12, nawonso anaona Yesu ataukitsidwa. Kenako Khristu “anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.” Mwina apa panali pamsonkhano wosangalatsa wotchulidwa pa Mateyu 28:16-20, umene unachitikira ku Galileya. Kenako Yesu “anaonekera kwa Yakobo.” N’kutheka kuti Yakobo ameneyu anali m’bale wake wa Yesu yemwe poyamba sankakhulupirira kuti iye ndi Mesiya. (Yoh. 7:5) Koma ataona kuti waukitsidwa, Yakobo anayamba kukhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya. N’zochititsa chidwi kuti cha m’ma 55 C.E. pamene Paulo ankalemba kalatayi, anthu ambiri amene anaona Yesu ataukitsidwa anali adakali ndi moyo. Choncho aliyense amene akanakayikira akanatha kufunsa anthu odalirika omwe anaona Yesu ataukitsidwa. w20.12 3 ¶5, 7-8
Lachiwiri, May 24
Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.—Sal. 41:3.
Tikamadwala, makamaka ngati matendawo atenga nthawi yaitali, mwina zingamativute kuti tiziona zinthu moyenera. Zikatere tizipempha Yehova kuti atithandize. N’zoona kuti iye sangatichiritse modabwitsa panopa, koma amatilimbikitsa ndi kutipatsa mphamvu kuti tithe kupirira. (Sal. 94:19) Mwachitsanzo, angalimbikitse abale ndi alongo athu kuti atithandize ntchito zapakhomo. Iye angalimbikitsenso abale athu kuti apemphere nafe limodzi kapenanso angatikumbutse mfundo zolimbikitsa zopezeka m’Mawu ake. Angatikumbutse zinthu zabwino zimene tikuyembekezera m’dziko latsopano monga moyo wabwino wopanda matenda kapena zopweteka zilizonse. (Aroma 15:4) Komabe mwina tingayambe kuona kuti sitingathe kuchita zambiri mu utumiki. Mlongo wina dzina lake Laurel anakhala m’mashini omuthandiza kupuma kwa zaka 37. Mlongoyu anapezekanso ndi khansa, matenda a pa khungu komanso anachitidwa maopaleshoni ambiri. Koma izi sizinamulepheretse kulalikira. Iye ankalalikira kwa manesi komanso anthu ena amene ankabwera kunyumba kwake ndipo anathandiza anthu pafupifupi 17 kuti aphunzire za Yehova. w20.12 24 ¶9; 25 ¶12
Lachitatu, May 25
Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?—Sal. 118:6.
Mtumwi Paulo ankafunika kuthandizidwa. Cha m’ma 56 C.E., khamu la anthu linamukokera kunja kwa kachisi ku Yerusalemu ndipo linkafuna kumupha. Tsiku lotsatira, pamene Paulo anamubweretsa ku Khoti Lalikulu la Ayuda, adani ake anatsala pang’ono kumukhadzulakhadzula. (Mac. 21:30-32; 22:30; 23:6-10) Pa nthawiyi mwina Paulo ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndipirira mavuto amenewa mpaka liti?’Kodi Yesu anathandiza bwanji Paulo? Tsiku limene Paulo anamangidwa, usiku “Ambuye” Yesu anaimirira pambali pake ndi kunena kuti: “Limba mtima! Pakuti wandichitira umboni mokwanira mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.” (Mac. 23:11) Zimenezitu zinalimbikitsa kwambiri Paulo. Yesu anayamikira Paulo chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anagwira ku Yerusalemu. Ndipo analonjeza kuti Paulo akafika bwinobwino ku Roma kuti akapitirize kugwira ntchito yochitira umboni kumeneko. Atamva zimenezi, Paulo anayamba kuona kuti ndi wotetezeka ngati mwana amene ali m’manja mwa bambo ake. w20.11 12 ¶1, 3; 13 ¶4
Lachinayi, May 26
Chiyembekezo chimene tili nachochi . . . , n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.—Aheb. 6:19.
Chiyembekezo chathu cha Ufumu chili “ngati nangula wa miyoyo yathu,” ndipo chimatithandiza kuti tisamatekeseke tikakumana ndi mavuto kapena zinthu zodetsa nkhawa. Muziganizira zimene Yehova watilonjeza m’tsogolo pa nthawi imene sipadzakhalanso chilichonse chotidetsa nkhawa. (Yes. 65:17) Muzidziyerekezera muli m’dziko latsopano la mtendere momwe simudzakhalanso zinthu zoipa. (Mika 4:4) Mukamauzanso ena zokhudza dziko latsopano mumayamba kukhulupirira kwambiri zimene mukuyembekezera. Muzichita zonse zimene mungathe mukamagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu. Kuchita zimenezi kungathandize “kuti chiyembekezo chanu chikhale chotsimikizika mpaka mapeto.” (Aheb. 6:11) Pamene mapeto a dziko loipali akuyandikira tizikumana ndi mavuto amene azitipangitsa kuti tizida nkhawa. Koma tikakumana ndi mavutowa tisamade nkhawa ndipo tizidalira Yehova osati kudalira mphamvu zathu. Tiyeni tiyesetse kuti zochita zathu zizisonyeza kuti tikukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”—Yes. 30:15. w21.01 7 ¶17-18
Lachisanu, May 27
Yehova ndi wachikondi chachikulu.—Yak. 5:11.
Lemba la Yakobo 5:11, limagwirizanitsa chikondi chachikulu cha Yehova ndi khalidwe lina limene limatithandiza kukhala naye pa ubwenzi, lomwe ndi chifundo. (Eks. 34:6) Njira imodzi imene Yehova amatisonyezera chifundo ndi kutikhululukira zimene timalakwitsa. (Sal. 51:1) M’Baibulo, kusonyeza chifundo kumaphatikizapo zambiri osati kungokhululukira chabe munthu amene watilakwira. Chifundo ndi khalidwe limene limasonyeza mmene timamvera mumtima tikaona munthu wina akuvutika, ndipo khalidweli limatipangitsa kuti tiyesetse kumuthandiza. Yehova amafotokoza kuti mmene amamvera pofuna kutithandiza zimaposa mmene mayi amamvera pofuna kuthandiza mwana wake. (Yes. 49:15) Tikakhala pa mavuto chifundo cha Yehova chimamuchititsa kuti atithandize. (Sal. 37:39; 1 Akor. 10:13) Tingasonyeze chifundo kwa abale ndi alongo athu tikamawakhululukira komanso tikamapewa kusunga chakukhosi akatilakwira. (Aef. 4:32) Koma njira yaikulu imene tingasonyezere chifundo kwa abale ndi alongo ndi kuwathandiza pamene akumana ndi mavuto. Tikamachita zimenezi timakhala tikutsanzira Yehova, yemwe ali ndi chikondi chachikulu kuposa wina aliyense.—Aef. 5:1. w21.01 21 ¶5
Loweruka, May 28
Khristu . . . anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.—1 Pet. 2:21.
Mwamuna ayenera kukhala wosamala kuti azichita zinthu moyenera. Iye safunika kutanganidwa kwambiri ndi ntchito pofuna kusamalira banja lake, mpaka kufika polephera kuthandiza anthu a m’banja lakewo kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kulephera kuwathandiza kuti aziona kuti ndi otetezeka ndiponso kuwaphunzitsa. Yehova amatiphunzitsa komanso kutipatsa malangizo n’cholinga choti zinthu zizitiyendera bwino. (Aheb. 12:7-9) Mofanana ndi Atate wake, nayenso Yesu amaphunzitsa mwachikondi anthu amene amawatsogolera. (Yoh. 15:14, 15) Iye amaperekanso uphungu koma mokoma mtima. (Mat. 20:24-28) Amadziwa kuti si ife angwiro ndipo nthawi zina timalakwitsa. (Mat. 26:41) Mwamuna yemwe amatsanzira Yehova ndi Yesu amakumbukira kuti anthu a m’banja lake si angwiro. Iye ‘samapsera mtima’ mkazi wake komanso ana ake. (Akol. 3:19) M’malomwake iye amagwiritsa ntchito mfundo y pa Agalatiya 6:1 ndipo amawalangiza ndi “mzimu wofatsa” pokumbukira kuti nayenso si wangwiro. Mofanana ndi Yesu, iye amadziwa kuti njira yabwino yophunzitsira anthu a m’banja lake ndi kudzera m’zochita zake. w21.02 6-7 ¶16-18
Lamlungu, May 29
Chopuma chilichonse chitamande Ya.—Sal. 150:6.
Yehova anagwiritsa ntchito dipo pogula moyo wa onse mumpingo komanso aliyense amene angakhulupirire Yesu. (Maliko 10:45; Mac. 20:28; 1 Akor. 15:21, 22) Choncho m’pomveka kuti Yehova anasankha Yesu yemwe anapereka moyo wake monga dipo kuti akhale mutu wampingo. N’chifukwa chake Yesu ali woyenera kupanga malamulo oti anthu, mabanja komanso aliyense mumpingo azitsatira, ndipo ali ndi udindo woonetsetsa kuti aliyense akutsatira malamulowo. (Agal. 6:2) Kuwonjezera pa kupanga malamulo palinso zambiri zimene Yesu amachita. Iye amatisamalira ndipo amakonda wina aliyense wa ife. (Aef. 5:29) Alongo amasonyeza kuti amalemekeza Khristu akamatsatira malangizo a amuna amene iye wawasankha kuti aziwatsogolera. Abale akamalemekeza alongo, amasonyeza kuti amamvetsa zimene Yehova anakonza zoti amuna azitsogolera. Ngati onse mumpingo kaya ndi amuna, akazi, mitu ya mabanja komanso akulu amamvetsa komanso kulemekeza zimene Yehova anakonza zoti ena azitsogolera, mumpingo mumakhala mtendere. Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti zimenezi zimathandiza kuti Atate wathu wakumwamba Yehova, azilemekezedwa. w21.02 18-19 ¶14-17
Lolemba, May 30
Davide anayamba kufunsira kwa Yehova.—1 Sam. 30:8.
Pa nthawi ina pomwe Davide ndi amuna omwe anali nawo ankakhala m’dera la Afilisiti pothawa Sauli, anasiya mabanja awo n’kupita kukamenya nkhondo. Kenako kunabwera adani kudzaukira mabanja awo, ndipo anawatenga n’kupita nawo monga akapolo. Davide akanatha kuganiza kuti popeza anali msilikali wodziwa kumenya nkhondo, ndiye kuti akanathanso kupeza njira yabwino yoti akapulumutse anthu omwe anatengedwawo. Koma iye anapempha Yehova kuti amuthandize kudziwa zoyenera kuchita. Davide anafunsira kwa Yehova kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la achifwambali?” Yehova anavomereza kuti Davide achite zimenezo ndipo anamutsimikizira kuti akapambana. (1 Sam. 30:7-10) Kodi mungaphunzirepo chiyani pa nkhaniyi? Achinyamata, muzifufuza kaye malangizo musanasankhe zochita. Muzipempha makolo anu kuti akuthandizeni. Mukhozanso kupeza malangizo abwino kwa akulu amene akhala akutumikira kwa nthawi yaitali. Yehova amawadalira akuluwa ndipo inunso mukhoza kumawadalira. Ndipotu iye amaona akulu monga “mphatso” mumpingo. (Aef. 4:8) Mukhoza kumasankha zinthu moyenera mukamatsanzira chikhulupiriro chawo komanso mukamamvera malangizo anzeru amene angakupatseni. w21.03 4-5 ¶10-11
Lachiwiri, May 31
[Palibe chingathe] kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu.—Aroma 8:38, 39.
Yesu ananena kuti ngati sitigwiritsa ntchito zimene timaphunzira, tingafanane ndi munthu amene wamanga nyumba yake pamchenga. Iye amagwira ntchito mwakhama, koma nthawi yake imangopita pachabe. Tikutero chifukwa ngati kutabwera mphepo kapena mvula yamphamvu, nyumbayo imagwa. (Mat. 7:24-27) Mofanana ndi zimenezi, ngati sitigwiritsa ntchito zimene tikuphunzira, tikhoza kungowononga nthawi yathu pachabe. Choncho tikamayesedwa kapena kuzunzidwa, chikhulupiriro chathu sichingakhale cholimba. Koma tikamaphunzira komanso kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo, timasankha zinthu mwanzeru, timakhala ndi mtendere wamumtima komanso chikhulupiriro chathu chimalimba. (Yes. 48:17, 18) Kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika tikamakumana ndi mayesero, tiyenera kudalira Yehova n’kumapemphera nthawi zonse komanso kumaphunzira Mawu ake. Ndipo tizikumbukira kuti chofunika kwambiri ndi kuchita zimene zingapangitse kuti Yehova alemekezedwe. Ndife otsimikiza kuti Yehova sadzatisiya ngakhale pang’ono ndipo palibe chimene wina aliyense angachite kuti amulepheretse kutikonda.—Aheb. 13:5, 6. w21.03 15 ¶6; 18 ¶20