June
Lachitatu, June 1
Tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo.—1 Ates. 2:8.
Monga aphunzitsi, tizisonyeza kuti timakonda ophunzira athu. Tiziwaona kuti posachedwa akhoza kudzakhala abale ndi alongo athu mumpingo. Tiyenera kudziwa kuti si zophweka kuti asiye kucheza ndi anzawo a poyamba komanso kuti asinthe zinthu zina pa moyo wawo n’kuyamba kutumikira Yehova. Choncho aphunzitsi abwino a Baibulo amathandiza ophunzira awo kuti adziwane ndi anthu ena mumpingo. Anthu amenewa angathandize ophunzirawo kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Zotsatira zake, ophunzirawo angasangalale kumagwirizana ndi anthu a Mulungu omwe angamawalimbikitse akakumana ndi mavuto. Muzithandiza ophunzirawo kuti aziona kuti ndi ofunika mumpingo ndiponso kuti ndi mbali ya banja lathu lauzimu. Tikufuna kuti wophunzira aliyense azisangalala kukhala m’banja la abale ndi alongo amene amakondana. Ndiyeno zingakhale zosavuta kuti wophunzirayo asiye kucheza ndi anthu amene sangamuthandize kuti azikonda Yehova. (Miy. 13:20) Ngati anthu amene ankacheza nawo poyamba atayamba kumusala, angadziwe kuti akhoza kupeza anzake abwino m’gulu la Yehova.—Maliko 10:29, 30; 1 Pet. 4:4. w20.10 17 ¶10-11
Lachinayi, June 2
Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.—Mat. 28:18.
Tiyenera kukhala anzake a Yesu kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Izi zili choncho pa zifukwa ziwiri. Choyamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Atateyo amakukondani, chifukwa munandikonda ine.” (Yoh. 16:27) Iye ananenanso kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yoh. 14:6) Kuyesetsa kukhala mnzake wa Yehova popanda kukhala mnzake wa Yesu kuli ngati kuyesetsa kulowa m’nyumba popanda kudzera pakhomo. Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo chimenechi pamene ananena kuti iye ndi “khomo la nkhosa.” (Yoh. 10:7) Chachiwiri, Yesu ankatsanzira ndendende makhalidwe a Atate ake. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Choncho njira yofunika yotithandiza kudziwa Yehova ndi kuphunzira za Yesu. Tikamaphunzira za Yesu timayamba kumukonda kwambiri. Ndipo tikayamba kukonda kwambiri Yesu tidzayambanso kukonda Atate ake. w20.04 21-22 ¶5-6
Lachisanu, June 3
Chotero ndimasangalala ndi kufooka, . . . pakuti pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.—2 Akor. 12:10.
Kodi panopa muli chigonere chifukwa cha matenda? Kapena kodi mumayenda pa njinga ya olumala? Kodi mawondo anu amangokhala njenjenje kapena mumavutika kuona bwinobwino? Ngati ndi choncho, kodi zingatheke kuthamanga limodzi ndi achinyamata amphamvu? Inde. Anthu ambiri achikulire komanso odwala akuthamanga panjira ya ku moyo. Iwo sadalira mphamvu zawo pochita zimenezi. M’malomwake, amadalira mphamvu za Yehova zomwe amazipeza akamamvetsera kapena kuonera misonkhano yochita kujambulidwa. Iwo amayesetsanso kulalikira kwa madokotala, manesi ndi achibale. Kaya mukukumana ndi vuto lotani, simuyenera kukhumudwa n’kumaganiza kuti simungathe kuthamanga panjira yopita ku moyo. Yehova amakukondani kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chanu komanso kupirira kumene mwasonyeza kwa zaka zambiri. Panopa m’pamene mukufunika kuthandizidwa kwambiri ndi Yehova ndipo iye sadzakusiyani. (Sal. 9:10) M’malomwake, adzakuyandikirani kwambiri. w20.04 29 ¶16-17
Loweruka, June 4
Ndikuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndiugawirenso kwa ena.—1 Akor. 9:23.
Kodi ndi nkhani ngati ziti zimene mungakambirane ndi anthu achipembedzo? Muziyesetsa kukambirana nawo zinthu zimene angagwirizane nazo. Mwachitsanzo, mwina amalambira Mulungu mmodzi, amavomereza kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu kapena mwina amakhulupirira kuti tikukhala m’dziko loipa lomwe liwonongedwe posachedwapa. Mukadziwa zimene munthu amakhulupirira, muzimulalikira mogwirizana ndi zimene angasangalale nazo. Muzikumbukira kuti anthu ena sakhulupirira mfundo zonse zimene chipembedzo chawo chimaphunzitsa. Choncho ngakhale mutadziwa chipembedzo cha munthu, yesetsani kudziwa zimene iyeyo amakhulupirira. M’bale wina yemwe ndi mmishonale ananena kuti anthu ena akhoza kunena kuti amakhulupirira za Mulungu Atate, mulungu Mwana ndi mulungu Mzimu Woyera. Koma mwina nawonso sakhulupirira kuti onsewa ali mwa Mulungu mmodzi. Iye anati: “Ndikazindikira zimenezi sindivutika kupeza nkhani zimene angagwirizane nazo.” Choncho tiyenera kuyesetsa kudziwa zimene anthu amakhulupirira. Kenako tikhoza kukhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana” ngati mmene Paulo ankachitira.—1 Akor. 9:19-22. w20.04 10 ¶9-10
Lamlungu, June 5
Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku adzapulumuka.—Dan. 12:1.
Tikamaganizira zam’tsogolo, sitiyenera kudera nkhawa chilichonse. Tikutero chifukwa Danieli komanso Yohane ananena kuti pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova ndi Yesu adzapulumutsa anthu amene amawatumikira. Danieli ananena kuti anthu omwe adzapulumuke ndi amene mayina awo ‘analembedwa m’buku.’ Ndiye kodi tingatani kuti dzina lathu lilembedwe m’buku limeneli? Tiyenera kusonyeza kuti timakhulupirira Yesu yemwe ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. (Yoh. 1:29) Tiyeneranso kudzipereka kwa Mulungu ndi kubatizidwa. (1 Pet. 3:21) Komanso tiyenera kusonyeza kuti tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu pothandiza ena kudziwa Yehova. Panopa tiyenera kudalira kwambiri Yehova, ndiponso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye komanso atumiki ake okhulupirika. Inoyonso ndi nthawi imene tiyenera kusonyeza kuti tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu. Tikamachita zimenezi, tidzapulumuka Ufumu wa Mulungu ukamadzawononga mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera. w20.05 16 ¶18-19
Lolemba, June 6
Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo mpaka kalekale.—Sal. 135:13.
Adamu ndi Hava ankadziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova komanso ankadziwa zambiri zokhudza Yehovayo. Ankadziwa kuti iye ndi Mlengi wawo yemwe anawapatsa moyo, malo okongola oti azikhala komanso banja labwino. (Gen. 1:26-28; 2:18) Koma kodi anapitiriza kuganizira zinthu zonse zimene Yehova anawachitira? Kodi anasonyezabe kuti amamukonda komanso kumuyamikira? Mayankho a mafunsowa anadziwika pamene mdani wa Mulungu anawayesa. Satana anachititsa njoka kuoneka ngati ikulankhula pamene anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” (Gen. 2:16, 17; 3:1) Funsoli linali ndi mfundo inayake yabodza imene inachititsa Hava kuyamba kuganiza zolakwika zokhudza Mulungu. Mulungu ananena kuti anthuwo akhoza kudya zipatso za mtengo uliwonse kupatulapo umodzi. (Gen. 2:9) Satana anapotoza dala zimene Yehova ananena. Iye ankafuna kuti Adamu ndi Hava aziona kuti Mulungu ndi woumira. N’kutheka kuti Hava anayamba kuganiza kuti, ‘Kapenatu Mulungu akutimana zinazake.’ w20.06 3-4 ¶8-9
Lachiwiri, June 7
Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.—Akol. 3:13.
Atumiki a Yehova ena anakhumudwitsidwa ndi Akhristu anzawo. Mtumwi Paulo ankadziwa kuti nthawi zina tikhoza kukhala ndi chifukwa chomveka “chodandaulira” zochita za m’bale kapena mlongo wina. N’kutheka kuti m’bale kapena mlongo angatichitiredi zinthu zopanda chilungamo koma ngati sitingasamale tikhoza kupsa mtima kwambiri. Munthu akakhumudwa akhoza kusiya kutumikira Yehova. Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wa ku South America, dzina lake Pablo. Munthu wina anamunamizira kuti wachita zinazake zoipa ndipo anachotsedwa paudindo. Kodi Pablo anatani? Iye anati: “Ndinakhumudwa kwambiri ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinafooka.” Enanso amafooka chifukwa choti nthawi ina anachita tchimo lalikulu ndiye amadziimbabe mlandu n’kumaona ngati Mulungu sangawakondenso. Ngakhale kuti analapa komanso anasonyezedwa chifundo, angamadzionebe kuti si oyenera kukhala atumiki a Mulungu. Kodi mumamva bwanji mukaganizira za abale ndi alongo omwe anakumana ndi zofanana ndi zimene takambiranazi? w20.06 19 ¶6-7
Lachitatu, June 8
Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.—Miy. 22:3.
Tiyenera kuzindikira zinthu zimene zingativulaze n’kumayesetsa kuzipewa. (Aheb. 5:14) Mwachitsanzo, timafunika kusankha zosangalatsa mwanzeru. Nthawi zambiri pa TV komanso m’mafilimu amaonetsa zinthu zachiwerewere. Mulungu sasangalala ndi zinthu zimenezi ndipo ngati munthu atapitiriza kuonera mafilimu amenewa, akhoza kugwera m’mavuto. Timapewa zosangalatsa zoterezi chifukwa zikhoza kutichititsa kuti tisiye kukonda Yehova. (Aef. 5:5, 6) Nafenso tiyenera kuzindikira kuopsa kwa nkhani zabodza zimene ampatuko amafalitsa. Iwo angatichititse kuti tiyambe kukayikira abale athu komanso gulu la Yehova. (1 Tim. 4:1, 7; 2 Tim. 2:16) Nkhani ngati zimenezi zingafooketse chikhulupiriro chathu. Tiyenera kupewa kukhulupirira mabodzawa. N’chifukwa chiyani tiyenera kutero? Chifukwa nkhani zabodzazi zimafalitsidwa ndi “anthu opotoka maganizo ndi osadziwa choonadi,” omwe cholinga chawo ndi “kukangana ndi anthu ndiponso kutsutsana pa mawu.” (1 Tim. 6:4, 5) Iwo amafuna kuti tizikhulupirira mabodza awowo n’kuyamba kukayikira abale athu. w20.09 29 ¶13, 15
Lachinayi, June 9
Musamangodzifunira zopindulitsa [inu nokha] basi, koma zopindulitsanso wina.—1 Akor. 10:24.
Anthu okwatirana ayenera kumalemekezana. (Aef. 5:33) Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala opatsa m’malo momangoyembekezera kulandira. (Mac. 20:35) Kodi ndi khalidwe liti limene lingathandize kuti anthu okwatirana azikondana komanso kulemekezana? Khalidwe lake ndi kudzichepetsa. Kudzichepetsa kwathandiza mabanja ambiri a Chikhristu kuti azikhala osangalala. Mwachitsanzo, mwamuna wina dzina lake Steven anati: “Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuchitira zinthu limodzi, makamaka pakakhala mavuto. M’malo moganizira kuti ‘n’chiyani chingandithandize?’ muziganizira kuti ‘n’chiyani chingatithandize?’” Mkazi wake Stephanie, ananenanso zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Palibe amene amafuna kukhala ndi munthu amene amangokhalira kukangana naye. Ndiye tikasemphana maganizo, timayesetsa kupeza chimene chayambitsa vutolo. Tikatero timapemphera, kufufuza mfundo zimene zingatithandize komanso kukambirana zimene tingachite. Timalimbana ndi vutolo osati kulimbana tokhatokha.” Anthu okwatirana amakhala osangalala ngati aliyense sadziona kuti ndi wofunika kuposa mnzake. w20.07 3-4 ¶5-6
Lachisanu, June 10
Ndinali kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa.—Agal. 1:14.
Sitiyenera kudalira mphamvu kapena luso lathu tikamatumikira Yehova. Mtumwi Paulo anali wophunzira kwambiri. Iye anaphunzitsidwa ndi mtsogoleri wachiyuda wolemekezeka kwambiri, dzina lake Gamaliyeli. (Mac. 5:34; 22:3) Ndipo pa nthawi ina, Paulo anali munthu wofunika kwambiri pakati pa Ayuda. (Mac. 26:4) Koma zimenezi sizinachititse Paulo kukhala wodzidalira. Paulo anasiya zinthu zonse zomwe zinkachititsa anthu a m’dzikoli kumuona kuti ndi wamphamvu. (Afil. 3:8) Iye anakumana ndi mavuto ambiri chifukwa chokhala wotsatira wa Khristu. Anthu a mtundu wake ankadana naye. (Mac. 23:12-14) Ndiponso anamenyedwa komanso kumangidwa ndi Aroma anzake. (Mac. 16:19-24, 37) Anazindikiranso kuti ankalephera kuchita zinthu zoyenera chifukwa chakuti anali wochimwa. (Aroma 7:21-25) Koma iye sanalole kuti adani ake komanso zimene ankalakwitsa zimusokoneze. M’malomwake ‘ankasangalala ndi kufooka’ kwake. N’chifukwa chiyani ankasangalala? Chifukwa pamene ankadzimva kuti wafooka m’pamene ankaona mmene Mulungu ankamuthandizira.—2 Akor. 4:7; 12:10. w20.07 16 ¶7-8
Loweruka, June 11
Wokhulupirira ine . . . adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi.—Yoh. 14:12.
Tiyenera kumaona kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi yofunika kwambiri masiku ano. Yesu ananeneratu kuti otsatira ake adzapitirizabe kulalikira pambuyo poti waphedwa ndipo adzalalikira kuposa mmene iyeyo anachitira. Ndiyeno ataukitsidwa, anathandiza ophunzira akewo kugwira nsomba zambiri. Atachita zimenezi, Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu ndi yofunika kwambiri kuposa ntchito ina iliyonse. (Yoh. 21:15-17) Atangotsala pang’ono kupita kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti ntchito yolalikira yomwe anayambitsayi, idzafalikira m’madera ambiri. (Mac. 1:6-8) Patapita zaka zambiri, Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya onena zimene zidzachitike mu “tsiku la Ambuye.” M’masomphenyawo Yohane anaona zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Iye anaona mngelo ali ndi “uthenga wabwino wosatha, woti aulengeze kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 1:10; 14:6) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tizigwira nawo ntchito yolakira, yomwe ikuchitika padziko lonse mpaka itafika kumapeto. w20.09 9 ¶5
Lamlungu, June 12
Mwa chikhulupiriro, pamene Abulahamu anayesedwa, zinali ngati wapereka kale Isaki nsembe.—Aheb. 11:17.
Abulahamu anakumana ndi mavuto m’banja mwake. Mkazi wake Sara anali wosabereka. Vutoli linachititsa kuti asamasangalale kwa zaka zambiri. Kenako Sara anapereka kapolo wake Hagara kwa Abulahamu kuti awaberekere ana. Koma Hagara ali ndi pakati pa Isimaeli, anayamba kuchitira chipongwe Sara. Zinthu zinafika poipa kwambiri mpaka Sara anathamangitsa Hagara.(Gen. 16:1-6) Patapita nthawi, Sara anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna yemwe anamupatsa dzina lakuti Isaki. Abulahamu ankakonda ana ake onse awiri, Isimaeli ndi Isaki. Koma chifukwa choti Isimaeli ankazunza Isaki, Abulahamu anakakamizika kuthamangitsa Isimaeli ndi Hagara. (Gen. 21:9-14) Patapita zaka, Yehova anauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wake Isaki. (Gen. 22:1, 2; Aheb. 11:17-19) Pa zochitika zonsezi Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza zokhudza ana ake. w20.08 4 ¶9-10
Lolemba, June 13
Valani umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.—Aef. 4:24.
Taganiziraninso mmene anthu oukitsidwawo adzasangalalire pamene azidzayesetsa kuvula umunthu wawo wakale kuti azimvera Mulungu. Anthu omwe adzasinthe zinthu pa moyo wawo, adzaloledwa kuti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Koma Yehova sadzalola kuti anthu omwe akukana kusintha akhalebe m’Paradaiso n’kumasokoneza mtendere. (Yes. 65:20; Yoh. 5:28, 29.) Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, anthu adzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Miyambo 10:22, omwe amati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.” Mothandizidwa ndi mzimu woyera, anthu a Mulungu adzakhala olemera mwauzimu kutanthauza kuti adzayamba kufanana kwambiri ndi Khristu ndipo pamapeto pake adzakhala angwiro. (Yoh. 13:15-17; Aef. 4:23) Komanso tsiku lililonse thanzi lawo lizidzawonjezereka ndipo adzakhala anthu abwino. Moyo udzakhalatu wosangalatsa kwambiri.—Yobu 33:25. w20.08 17 ¶11-12
Lachiwiri, June 14
Muyesetse . . . kusalowerera mu nkhani za eni.—1 Ates. 4:11.
Tizikumbukira kuti Akhristu ena anasankha kusakhala pabanja. Ena amafuna atakhala pabanja koma sanapeze munthu woyenera kukwatirana naye. Pamene enanso, mkazi kapena mwamuna wawo anamwalira. Mulimonse mmene zingakhalire, kodi n’koyenera kuti Akhristu azifunsa abale ndi alongo amenewa chifukwa chimene sali pabanja kapena kuyesa kuwathandiza kupeza munthu woti akwatirane naye? N’kutheka kuti ena mwa Akhristuwa angapemphe kuti ena awathandize kupeza wokwatirana naye. Koma ngati sanapemphe thandizo, kodi Akhristuwa angamve bwanji ngati wina atayesa kuwapezera munthu woti akwatirane naye? (1 Tim. 5:13) Abale komanso alongo omwe sali pabanja angasangalale kwambiri tikamawaona kuti ndi ofunika chifukwa cha makhalidwe awo abwino. Koma angakhumudwe tikamawamvera chisoni chifukwa choti sali pabanja. Choncho m’malo mochita zimenezi, tiziwayamikira chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Tikamachita zimenezi, abale ndi alongo athu omwe sali pabanja sangamaone ngati tikuwauza kuti: ‘Tilibe nanu ntchito.’ (1 Akor. 12:21) Ndipo angadziwe kuti timawalemekeza komanso timawaona kuti ndi ofunika kwambiri mumpingo. w20.08 29 ¶10, 14
Lachitatu, June 15
[Khristu] anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.—1 Akor. 15:6.
Patapita nthawi, Yesu anaonekera kwa mtumwi Paulo. (1 Akor. 15:8) Paulo (Saulo) anali paulendo wopita ku Damasiko pamene anamva mawu a Yesu ndi kuona masomphenya a Yesuyo ali kumwamba. (Mac. 9:3-5) Zimene zinachitikira Paulo zinapereka umboni winanso wotsimikizira kuti Yesu anaukitsidwadi. (Mac. 26:12-15) Anthu ena akanachita chidwi kwambiri ndi umboni wa Paulo chifukwa choti poyamba iye ankazunza Akhristu. Paulo atakhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa, anayesetsa kuthandiza anthu ena kuti akhulupirirenso zimenezi. Pamene Paulo ankalalikira zoti Yesu anafa kenako n’kuukitsidwa, anakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kumenyedwa, kuikidwa m’ndende komanso kusweka kwa chingalawa. (1 Akor. 15:9-11; 2 Akor. 11:23-27) Paulo ankakhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa moti anali wokonzeka kufa chifukwa cholalikira zimene ankakhulupirirazo. Kodi umboni wochokera kwa Akhristu oyambirirawa, sukutithandiza kuti ifenso tizikhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa? Ndipotu umboni umenewu umatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti m’tsogolomunso amene anamwalira adzaukitsidwa. w20.12 3 ¶8-10
Lachinayi, June 16
Mukamufunafuna [Yehova], iye adzalola kuti mum’peze.—2 Mbiri 15:2.
Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimafika pamisonkhano nthawi zonse?’ Tikakhala pamisonkhano timapeza mphamvu zotithandiza kuti tipitirizebe kutumikira Yehova. (Mat. 11:28) Tingadzifunsenso kuti, ‘Kodi ndimaphunzira Baibulo pandekha nthawi zonse?’ Ngati mumakhala ndi banja lanu, kodi mumachita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse? Kapena ngati mumakhala nokha, kodi mumapeza nthawi yoti muziphunzira Mawu a Mulungu mlungu uliwonse? Komanso kodi mumayesetsa kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu? N’chifukwa chiyani tikufunika kudzifunsa mafunso amenewa? Baibulo limanena kuti Yehova amafufuza zimene zili m’maganizo mwathu komanso m’mitima yathu. Nafenso tiyenera kuchita zomwezo. (1 Mbiri 28:9) Ndiye tikaona kuti tikufunika kusintha zolinga zimene tili nazo, komanso mmene timaganizira tizipempha Yehova kuti atithandize. Inoyo ndi nthawi yoti tizikonzekera mayesero amene akubwera kutsogolo. w20.09 19 ¶19-20
Lachisanu, June 17
Palibe aliyense wolephera kulekana ndi chuma chake chonse amene angathe kukhala wophunzira wanga.—Luka 14:33.
Yesu anafotokoza fanizo losonyeza zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale wophunzira wake. Iye anafotokoza za munthu amene akufuna kumanga nsanja komanso za mfumu imene ikufuna kupita kunkhondo. Yesu ananena kuti munthuyo amafunika kuyamba “wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge” kuti aone ngati angamalize kumanga nsanjayo. Komanso mfumuyo iyenera kuyamba “yakhala pansi ndi kuganiza mofatsa” kuti ione ngati asilikali ake ali okonzeka kumenya nkhondoyo. (Luka 14:27-32) Mofanana ndi zimenezi, Yesu ankadziwa kuti munthu amene akufuna kukhala wophunzira wake amafunika kufufuza mosamala kuti adziwe zimene wotsatira wa Yesu amayenera kuchita. Choncho tiyenera kumalimbikitsa anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti azipeza nthawi yoti tiziphunzira nawo mlungu uliwonse. Monga mphunzitsi, muyenera kukonzekera bwino musanapite kukaphunzira ndi munthu Baibulo. Muziganiziranso wophunzira Baibulo wanuyo, n’kuona mmene mungamufotokozere mfundozo mosavuta ndi momveka bwino kuti athe kuzimvetsa komanso kuzigwiritsa ntchito pa moyo wake.—Neh. 8:8; Miy. 15:28a. w20.10 7 ¶5; 8 ¶7
Loweruka, June 18
Choncho pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.—Mat. 28:19, 20.
Malangizo amene Yesu anapereka ndi omveka bwino. Ananena kuti tiziphunzitsa anthu zimene iyeyo analamula. Komabe, sitiyenera kuiwala mfundo yofunika yomwe anatchula. Yesu sananene kuti: ‘Muziwaphunzitsa zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.’ M’malomwake ananena kuti: Muziwaphunzitsa “kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” Kuti titsatire malangizo a Yesuwa, tiyenera kuphunzitsa ophunzira athu zimene ayenera kuchita komanso tiyenera kuwasonyeza mmene angachitire zimenezo. (Mac. 8:31) “Kusunga” lamulo kumatanthauza kumvera lamulolo. Tikamaphunzira Baibulo ndi anthu ena, timawaphunzitsa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. Koma pali zinanso zimene tingachite. Tiyenera kuwaphunzitsa kuti azitsatira zimene akuphunzirazo. (Yoh. 14:15; 1 Yoh. 2:3) Zochita zathu zingasonyeze ophunzira athu mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Malemba akakhala kusukulu, kuntchito kapena akamachita zosangalatsa. Muzipemphera limodzi ndi ophunzira anu, kupempha Yehova kuti aziwatsogolera ndi mzimu wake woyera.—Yoh. 16:13. w20.11 2-3 ¶3-5
Lamlungu, June 19
“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,” watero Yehova wa makamu.—Zek. 4:6.
Ophunzira a Yesu ankakumananso ndi mavuto. Mwachitsanzo, iwo anali ndi mipukutu yochepa. Komanso analibe zinthu zina ndi mabuku owathandiza kumvetsa Baibulo ngati zilili masiku ano. Ophunzirawo ankafunika kulalikira kwa anthu ambiri amene ankalankhula zinenero zosiyanasiyana. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, iwo anachita zinthu zosayembekezereka. M’zaka zochepa anali atalalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:6, 23) Masiku athu ano. Yehova akupitirizabe kutsogolera komanso kupereka mphamvu kwa anthu ake. Njira yaikulu imene amagwiritsa ntchito potsogolera anthu ndi Baibulo, lomwe linauziridwa ndi mzimu woyera. M’Baibulo timapezamo nkhani yonena za utumiki wa Yesu komanso lamulo limene anapereka kwa otsatira ake, loti apitirize kugwira ntchito imene anayambitsa. (Mat. 28:19, 20) Yehova ndi Mulungu wopanda tsankho iye ananeneratu kuti uthenga wabwino udzalalikidwa ku “fuko lililonse chinenero chilichonse ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6, 7) Iye amafuna kuti munthu aliyense akhale ndi mwayi womva uthenga wa Ufumu. w20.10 21 ¶6-8
Lolemba, June 20
Anthu odzichepetsa mudzawapulumutsa. Koma mumatsutsa odzikweza.—2 Sam. 22:28.
Mfumu Davide inkakonda “chilamulo cha Yehova.” (Sal. 1:1-3) Iye ankadziwa kuti Yehova amapulumutsa anthu odzichepetsa koma amatsutsa odzikweza.Choncho analola kuti malamulo a Yehova amuthandize kusintha maganizo ake. Iye analemba kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera. (Sal. 16:7) Ngati ndife odzichepetsa, tidzalola kuti Mawu a Mulungu atithandize kusintha maganizo athu olakwika tisanachite zoipa. Zingakhale ngati tikumva Mawu a Mulungu akutiuza kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.” Mawu a Mulunguwa angatichenjeze tikayamba kuchoka panjirayi kulowera kudzanja lamanzere kapena lamanja. (Yes. 30:21) Kumvera Yehova kumatithandiza m’njira zambiri. (Yes. 48:17) Mwachitsanzo, kumatithandiza kupewa kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti wina atipatse uphungu, zomwe n’zochititsa manyazi. Ndiponso kumatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa timadziwa kuti amatisamalira monga mwana wake wokondedwa.—Aheb. 12:7. w20.11 20 ¶6-7
Lachiwiri, June 21
Atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka monyodola.—Mac. 17:32.
Mwina anthu ena ku Korinto anatengera maganizo amenewa. (1 Akor. 15:12) N’kutheka kuti ena ankaganiza kuti anthu amaukitsidwa mophiphiritsa. Iwo ankaona kuti munthu amakhala wakufa chifukwa choti ndi wochimwa koma akakhala Mkhristu amakhala ndi moyo chifukwa machimo ake amakhululukidwa. Kaya sankakhulupirira pa zifukwa zotani, kukana kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa kunapangitsa kuti chikhulupiriro chawo chikhale chopanda ntchito. Ngati Mulungu sanaukitse Yesu ndiye kuti dipo silinaperekedwe ndipo machimo a anthu onse sanakhululukidwe. Choncho amene ankatsutsa zoti akufa adzaukitsidwa analibe chiyembekezo chenicheni. (1 Akor. 15:13-19; Aheb. 9:12, 14) Mtumwi Paulo ankadziwa kuti Khristu “anaukitsidwa kwa akufa.” Kuukitsidwa kumeneku kunali kwapadera kuposa kwa anthu amene anaukitsidwa m’mbuyomu chifukwa patapita nthawi anthuwo anafanso. Paulo ananena kuti Yesu anali “chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” Iye anali woyamba kuukitsidwa ndi thupi lauzimu komanso anali woyamba kupita kumwamba.—1 Akor. 15:20; Mac. 26:23; 1 Pet. 3:18, 22. w20.12 5 ¶11-12
Lachitatu, June 22
Anali kupatsa okhulupirira a kumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu . . . anagamula.—Mac. 16:4.
M’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulira ku Yerusalemu, linkagwira ntchito mogwirizana kuti anthu a Mulungu azichita zinthu mwadongosolo komanso azikhala mwamtendere. (Mac. 2:42) Mwachitsanzo, pamene nkhani ya mdulidwe inabuka cha m’ma 49 C.E., abale a m’bungwe lolamulira motsogoleredwa ndi mzimu woyera anakambirana nkhaniyi. Nkhaniyi ikanapanda kuthetsedwa, abale akanakhala ogawanika ndipo zimenezi zikanachititsa kuti ntchito yolalikira isamayende bwino. Komanso ngakhale kuti atumwi ndi akuluwo anali a mtundu wa Chiyuda sanalole kusokonezedwa ndi miyambo ya Chiyuda kapena anthu amene ankalimbikitsa miyamboyi. M’malomwake iwo anadalira Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera kuti uwatsogolere posankha zochita. (Mac. 15:1, 2, 5-20, 28) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yehova anadalitsa zimene anasankha, mpingo unapitiriza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana ndipo ntchito yolalikira inapitiriza kuyenda bwino. (Mac. 15:30, 31; 16:4, 5) Masiku anonso, gulu la Yehova limathandiza Akhristu m’mipingo yonse kuti azichita zinthu mwadongosolo komanso kuti azikhala mwamtendere. w20.10 22-23 ¶11-12
Lachinayi, June 23
Solomo mwana wanga, [ndi] amene Mulungu wamusankha.—1 Mbiri 29:1.
Nthawi zina sitingapatsidwe utumiki winawake chifukwa cha uchikulire, matenda kapena chifukwa cha zinthu zina. Ngati zinthu zili choncho pa moyo wathu tingaphunzire zambiri kuchokera kwa Mfumu Davide. Davide ankafunitsitsa kuti agwire ntchito yomanga kachisi koma atauzidwa kuti Mulungu sanamusankhe kuti agwire ntchitoyi, anathandiza ndi mtima wonse munthu amene Mulungu anamusankha kuti agwire ntchitoyo. Iye anapereka golide ndi siliva wambiri kuti agwiritsidwe ntchito pomanga kachisiyo. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. (2 Sam. 7:12, 13; 1 Mbiri 29:3-5) Chifukwa cha matenda, m’bale wina wa ku France dzina lake Hugues, anasiya kutumikira ngati mkulu komanso sankatha ngakhale kugwira ntchito zing’onozing’ono zapakhomo. Iye analemba kuti: “Poyamba ndinakhumudwa kwambiri ndipo ndinkangodziona ngati wachabechabe. Patapita nthawi ndinaona kuti ndi bwino kuti ndisamadandaule chifukwa cha zinthu zimene sindinkakwanitsa kuchita. Nditatero ndinayamba kusangalala ndi zimene ndinkakwanitsa kuchita potumikira Yehova. Mofanana ndi Gidiyoni ndi amuna 300 omwe anali otopa, ndipitirizabe kumenya nkhondo.”—Ower. 8:4. w20.12 25 ¶14-15
Lachisanu, June 24
Tipitirize kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Pofotokoza za moyo wa Yesu, mtumwi Yohane anagwiritsa ntchito kwambiri mawu akuti “chikondi” kuposa anzake atatu amene analembanso Uthenga Wabwino. Zimene Yohane anauziridwa kulemba zimatithandiza kudziwa kuti Akhristu ayenera kusonyeza chikondi pa zochita zawo zonse. (1 Yoh. 4:10, 11) Komabe, zinamutengera nthawi Yohane kuti azindikire mfundo imeneyi. Pamene Yohane anali wachinyamata, nthawi zina zinkamuvuta kusonyeza chikondi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yesu ndi ophunzira ake ankapita ku Yerusalemu ndipo anadutsa ku Samariya. Anthu a m’mudzi wina wa ku Samariyako sanawalandire bwino. Yohane anauza Yesu kuti apemphe moto kuti utsike kuchokera kumwamba ndi kuwononga anthu onse a m’mudzi umenewo. (Luka 9:52-56) Pa nthawi inanso, Yohane ndi m’bale wake Yakobo ananyengerera mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Atumwi enawo atadziwa zimene Yakobo ndi Yohane anachita, anakwiya kwambiri. (Mat. 20:20, 21, 24) Koma ngakhale kuti Yohane ankalakwitsa zinthu zina, Yesu ankamukondabe.—Yoh. 21:7. w21.01 8-9 ¶3-4
Loweruka, June 25
Khristu sanadzikondweretse yekha.—Aroma 15:3.
Yehova amasankha zinthu zimene zingakhale zabwino kwa onse. Mwachitsanzo, iye anatilenga osati n’cholinga chofuna kupeza zinazake, koma kuti nafenso tizisangalala ndi moyo. Ndipotu palibe akanamukakamiza kupereka Mwana wake chifukwa cha machimo athu. Koma mwakufuna kwake iye anachita zimenezi kuti atithandize. Nayenso Yesu ankasankha zinthu zimene zinkathandiza ena. Mwachitsanzo, pa nthawi ina iye atatopa anasankha kupitirizabe kuphunzitsa anthu m’malo mopita kukapuma. (Maliko 6:31-34) Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja wabwino amadziwa kuti chimodzi mwa zinthu zovuta kwambiri ndi kusankha mwanzeru zinthu zokhudza banja lake ndipo saiona mopepuka nkhani imeneyi. Iye amapewa kusankha zinthu mopupuluma kapena potengera mmene akumvera pa nthawiyo. M’malomwake iye amalola kuti Yehova azimuphunzitsa kusankha bwino zochita. (Miy. 2:6, 7) Akamachita zimenezi amaganizira zimene zingathandizenso ena, osati iye yekha. (Afil. 2:4) Mwamuna akamayesetsa kutsanzira Yehova ndi Yesu, angathe kukhala mutu wa banja wabwino. w21.02 7 ¶19-21
Lamlungu, June 26
Asa anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.—2 Mbiri 14:2.
Mfumu Asa ali wachinyamata anali wodzichepetsa komanso wolimba mtima. Mwachitsanzo, bambo ake Abiya atamwalira, Asa anayamba kulamulira ndipo anayamba kuchotsa mafano onse m’dzikolo. Komanso “anauza Ayuda kuti afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira Chilamulo.” (2 Mbiri 14:1-7) Ndiponso Zera Mwitiyopiya atabwera kudzamenyana nawo ndi asilikali ake 1 miliyoni, Asa anachita zinthu mwanzeru popempha Yehova kuti awathandize. Iye anati: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Asa ankakhulupirira kwambiri kuti Yehova awapulumutsa. Choncho Asa ankadalira kwambiri Atate wake wakumwamba ndipo “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo.” (2 Mbiri 14:8-12) Mungavomereze kuti zinali zoopsa kwambiri kwa Asa kuti amenyane ndi gulu la asilikali 1 miliyoni. Koma chifukwa chakuti iye anadalira Yehova anapambana. w21.03 5 ¶12-13
Lolemba, June 27
Khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu.—Aroma 12:10.
Baibulo limatifotokozera nkhani za anthu amene ankakondana kwambiri. Taganizirani chitsanzo cha Yonatani ndi Davide. Baibulo limati: “Yonatani anagwirizana kwambiri ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.” (1 Sam. 18:1) Yehova anali atasankha Davide kuti adzakhale mfumu m’malo mwa Sauli. Zitatero Sauli anayamba kuchitira nsanje Davide ndipo ankafuna kumupha. Koma Yonatani sanafune kuthandiza bambo ake pofuna kukwaniritsa cholinga chawo chofuna kupha Davide. M’malomwake iye analonjezana ndi Davide kuti adzapitiriza kukhala mabwenzi komanso kuti nthawi zonse azithandizana. (1 Sam. 20:42) N’zochititsa chidwi kuti Yonatani ndi Davide ankagwirizana kwambiri ngakhale kuti panali zinthu zambiri zimene zikanawalepheretsa kuti akhale mabwenzi. Mwachitsanzo, Yonatani ankasiyana ndi Davide ndi zaka pafupipafupi 30. Iye akanatha kuganiza kuti sangakhale mnzake wa munthu amene ndi wamng’ono kwa iye komanso alibe luso lililonse pa moyo. Koma iye sanaganize zimenezi ndipo ankamulemekeza kwambiri Davide. w21.01 21-22 ¶6-7
Lachiwiri, June 28
Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana.—Yak. 1:2.
Yesu analonjeza otsatira ake kuti adzapeza chimwemwe chenicheni. Koma anachenjezanso kuti onse amene amamukonda adzakumana ndi mayesero. (Mat. 10:22, 23; Luka 6:20-23) Timakhala osangalala chifukwa chokhala ophunzira a Khristu. Koma kodi timamva bwanji ngati anthu a m’banja lathu akutitsutsa chifukwa choti tikutumikira Yehova, akuluakulu a boma akamatizunza komanso anzathu a kuntchito kapena kusukulu akamatikakamiza kuti tichite zinthu zoipa? Kunena zoona zochitika ngati zimenezi zingatichititse kuti tizida nkhawa. Anthu ambiri amaona kuti kuzunzidwa si chifukwa chimene chingawapangitse kukhala osangalala. Komatu izi ndi zimene mawu a Mulungu amanena. Mwachitsanzo, mtumwi Yakobo analemba kuti m’malo moti tizida nkhawa tikakumana ndi mayesero, tizisangalala. (Yak. 1:2, 12) Komanso Yesu ananena kuti tizisangalala pamene tikuzunzidwa. (Mat. 5:11) Yehova anauzira mtumwi Yakobo kuti alembere Akhristuwa malangizo amene akanawathandiza kuti apitirizebe kukhala osangalala ngakhale pamene akukumana ndi mayesero. w21.02 26 ¶1-2; 27 ¶5
Lachitatu, June 29
[Upewe] nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera.—1 Tim. 6:20.
Mu nthawi ya Timoteyo, Akhristu ena sanayamikire mwayi umene anali nawo wokhala antchito anzake a Mulungu. Ena mwa Akhristu amenewa anali Dema Fugelo, Heremogene Hemenayo, Alekizanda ndi Fileto. (1 Tim. 1:19, 20; 2 Tim. 1:15; 2:16-18; 4:10) Poyamba anthu onsewa ankakonda Yehova, koma kenako anasiya kuona kuti zinthu zimene anapatsidwa ndi zamtengo wapatali. Kodi Satana amachita zotani pofuna kutitayitsa zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa? Tiyeni tione zina mwa njira zimene amagwiritsa ntchito. Iye amagwiritsa ntchito zosangalatsa komanso zinthu ngati TV, mafilimu, intaneti, manyuzipepala, mabuku ndi magazini. Amachita zimenezi pofuna kutichititsa kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu m’njira imene ingachititse kuti tisiye kukonda Yehova ndiponso kumvera malamulo ake. Iye amayesa kutiopseza pogwiritsa ntchito anzathu kapena kutizunza kuti tisiye kulalikira. Amayesanso kutikopa kuti tizimvetsera zinthu zimene ampatuko “monama amati ndiye ‘kudziwa zinthu,’” n’cholinga choti tisiye choonadi. Ngati sitingasamale, tingayambe kusiya choonadi pang’onopang’ono.—1 Tim. 6:21. w20.09 27 ¶6-8
Lachinayi, June 30
Yehova adzamva ndithu pempho langa loti andikomere mtima. Yehova adzalandira pemphero langa.—Sal. 6:9.
Kodi mnzanu kapena wachibale wanu anakukhumudwitsani chifukwa cholephera kukhala wokhulupirika kwa inu? Ngati ndi choncho mungapindule mukamawerenga nkhani ya Mfumu Davide ndi mwana wake Abisalomu. (2 Sam. 15:5-14, 31; 18:6-14) Mukuganizira mfundo zimenezi, muzimuuza Yehova mmene mukumvera chifukwa cha zoipa zimene ena akuchitirani. (Sal. 6:6-8) Tsopano ganizirani mmene Davide ankamvera pamene zonsezi zinkamuchitikira. Iye ankakonda kwambiri Abisalomu ndipo ankakhulupirira Ahitofeli. Komatu awiri onsewa, analephera kukhala okhulupirika kwa iye. Iwo anamukhumudwitsa kwambiri ndipo anafika mpaka pofuna kumupha. Davide akanatha kusiya kukhulupirira anzake ena onse n’kumakayikira kuti mwina nawonso ali kumbali ya Abisalomu. Akanatha kumangoganizira zake zokha mwinanso kuganiza zongothawa yekha m’dzikolo. Davide akanathanso kumangodziona ngati wolephera. M’malomwake anapemphera kwa Yehova. Anapemphanso anzake kuti amuthandize. Komanso anachita mwamsanga zimene anasankha. Iye anapitiriza kukhulupirira Yehova komanso anzake. w21.03 15 ¶7-8; 17 ¶10-11