July
Lachisanu, July 1
Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.—Mat. 28:18.
Tiyenera kukhala anzake a Yesu kuti mapemphero athu aziyankhidwa. Kungonena mawu akuti “m’dzina la Yesu” m’mapemphero athu si kokwanira. Koma tiyenera kudziwa mmene Yehova amagwiritsira ntchito Yesu poyankha mapemphero athu. Yesu anauza atumwi kuti: “Chilichonse chimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzachichita.” (Yoh. 14:13) N’zoona kuti Yehova ndi amene amamvetsera komanso kuyankha mapemphero athu koma wapatsa Yesu udindo wochita zimene Yehovayo wasankha. Choncho Mulungu asanayankhe mapemphero athu amaona kaye ngati timatsatira malangizo a Yesu. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani. Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.” (Mat. 6:14, 15) Choncho tiyenera kukomera mtima anthu ena ngati mmene Yehova ndi Yesu amachitira ndi ifeyo. w20.04 22 ¶6
Loweruka, July 2
Tikulengeza uthenga wabwino kwa inu. Tikuchita izi kuti musiye zachabechabe zimenezi ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo.—Mac. 14:15.
Mtumwi Paulo ankasintha uthenga wake kuti ugwirizane ndi zimene anthu amakonda. Mwachitsanzo, atafika ku Lusitara anapeza anthu amene sankadziwa kwenikweni za Malemba. Choncho iye anakambirana nawo nkhani zimene iwo ankazidziwa. Anakambirana nawo za zokolola komanso zinthu zina zosangalatsa. Iye ankagwiritsa ntchito mawu komanso zitsanzo zimene anthuwo akanamvetsa mosavuta. Muziyesetsa kuzindikira zimene anthu amakonda m’gawo lanu n’kusintha uthenga wanu kuti ugwirizane ndi zimenezo. Kodi mungadziwe bwanji zimene munthu amakonda? Chofunika ndi kukhala tcheru. Kodi munthuyo akulima, kuwerenga buku, kukonza galimoto kapena kuchita zinthu zina? Ndiyeno ngati n’zotheka muziyamba n’kukambirana zimene akuchitazo. (Yoh. 4 7) Mukhoza kudziwanso zambiri pongoona zimene munthu wavala. Mwina zingasonyeze dziko limene akuchokera, ntchito yake kapena timu ya masewera imene amaikonda. w20.04 11 ¶11-12
Lamlungu, July 3
Chitani zimenezi pamene mukumutulira [MulunguA] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.—1 Pet. 5:7.
Chifukwa cha matenda a nkhawa, abale ndi alongo ena amavutika kwambiri kuchita zinthu ndi anthu ena. Ngakhale kuti zimawavuta kukhala pa gulu, amapezekabe pamisonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu. Mwina amavutikanso kulankhula ndi anthu osawadziwa, koma amalalikirabe. Ngati ndi mmene zilili ndi inuyo, dziwani kuti si inu nokha. Anthu ambiri amavutika ndi zimenezi. Musaiwale kuti Yehova amasangalala mukamachita zonse zimene mungakwanitse. Popeza mukupitiriza kuchita zimene mungathe, ndiye kuti Yehova akukupatsani mphamvu imene mukufunikira. (Afil. 4:6, 7) Ngati mukutumikira Yehova ngakhale kuti mukulimbana ndi mavuto enaake, musamakayikire kuti iye akusangalala nanu. Ambirife sitikupeza bwino koma tikuthamangabe. (2 Akor. 4:16) Ndipo Yehova akhoza kutithandiza tonsefe kuti tithamange mpaka pa mapeto pa mpikisanowu. w20.04 31 ¶20-21
Lolemba, July 4
Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.—Aroma 1:20.
Timazindikira kuti Mulungu ndi wanzeru kwambiri tikaona mmene analengera dziko lapansili. (Aheb. 3:4) Dziko lapansi ndi limodzi mwa mapulaneti ambiri omwe amazungulira dzuwa. Koma dziko lathuli ndi pulaneti lapadera kwambiri chifukwa lili ndi zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo. Tingayerekezere dziko lapansili ndi sitima yodzaza ndi anthu yomwe ikuyenda pakatikati panyanja. Koma tingati pali kusiyana kwakukulu pakati pa sitima imeneyi ndi dziko lathu lapansili. Mwachitsanzo, kodi anthu amene ali musitimayi angakhale ndi moyo kwa nthawi yaitali bwanji ngati atamafunika kukonza okha mpweya, chakudya, madzi komanso ngati akungotaya zinyalala m’sitima momwemo? Sangakhale ndi moyo kwa nthawi yaitali. Komatu padzikoli anthu komanso zinyama mabiliyoni zikutha kukhala ndi moyo. Dzikoli limatulutsa mpweya, chakudya komanso madzi okwanira ndipo zinthuzi zimakhalapo nthawi zonse. Ngakhale kuti zinyalala zimatayidwa padziko lomweli, dzikoli limakhalabe lokongola komanso labwino kukhalapo. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Yehova anakonza dziko lapansili m’njira yoti zinthu zomwe zatha ntchito, zithe kukonzedwa ndi kugwiritsidwanso ntchito. w20.05 20 ¶3-4
Lachiwiri, July 5
Kufa simudzafa ayi.—Gen. 3:4.
Satana anayamba kudetsa dzina la Mulungu pouza Hava kuti Yehova ndi wabodza. Pamenepatu iye anakhala Mdyerekezi kapena kuti wonenera ena zoipa. Satana anakwanitsadi kupusitsa Hava chifukwa anamukhulupirira. (1 Tim. 2:14) Hava anayamba kukhulupirira kwambiri Satana kuposa Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti Hava asankhe kuchita zinthu molakwika kwambiri. Iye anasankha kusamvera Yehova moti anadya chipatso chimene anamuletsa. Pambuyo pake, anapatsanso Adamu chipatsocho. (Gen. 3:6) Tangoyesani kuganizira zimene Hava akanauza Satana. Bwanji ngati akanamuuza kuti: “Sindikukudziwa, ine ndimadziwa Yehova amene ndi Atate wanga komanso ndimamukonda ndi kumukhulupirira kwambiri. Zinthu zonse zomwe tili nazozi anatipatsa ndi iyeyo. Ndiye iweyo ukundiuza kuti Mulungu ndi woipa? Choka apa!” Kodi mukuganiza kuti Yehova akanamva bwanji kumva Hava akulankhula mawu amenewa osonyeza kuti amamukhulupirira kwambiri? (Miy. 27:11) Koma n’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava analephera kukhala okhulupirika. Chifukwa chakuti chikondi chawo kwa Mulungu chinali chitachepa, sakanathanso kuteteza dzina lake kuti lisadetsedwe. w20.06 4 ¶10-11
Lachitatu, July 6
Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.—Sal. 68:11.
Tiyenera kumayamikira alongo athu chifukwa cha zonse zimene amachita potumikira Yehova. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo kumanga komanso kukonza malo olambirira, kulalikira ndi magulu a zinenero za m’mayiko ena komanso kudzipereka kuti atumikire pabeteli. Enanso amagwira nawo ntchito zothandiza ena pakagwa ngozi zachilengedwe, amathandiza kumasulira nawo mabuku, komanso kutumikira ngati apainiya komanso amishonale. Kuonjezera pamenepa akazi amathandiza amuna awo, kuti akwanitse maudindo awo mumpingo komanso m’gulu la Yehova. Abale amenewa ndi “mphatso za amuna” ndipo amachita zambiri pothandiza ena. Komabe zikanakhala zovuta kwambiri kuti azikwanitsa kuchita zimenezi zikanakhala kuti akazi awo sawathandiza. (Aef. 4:8) Akulu ozindikira amaona kuti alongo “ndi khamu lalikulu” la anthu odzipereka ndipo nthawi zambiri ndi amene amachita bwino kwambiri pogwira ntchito yolalikira. Komanso akulu amazindikira kuti alongo olimba mwauzimu amakhala ndi luso lothandiza alongo achitsikana akamakumana ndi mavuto. (Tito 2:3-5) Apatu n’zoonekeratu kuti tiyenera kumayamikira alongo mumpingo. w20.09 23-24 ¶13-14
Lachinayi, July 7
Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.—Mat. 18:14.
Yehova saiwala anthu amene anamutumikirapo koma anasiya. Komanso samaiwala zimene anachita pomutumikira. (Aheb. 6:10) Mneneri Yesaya anafotokoza fanizo labwino losonyeza mmene Yehova amasamalirira anthu ake. Analemba kuti: “Iye adzaweta gulu lake la nkhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” (Yes. 40:11) Kodi Yehova, yemwe ndi M’busa Wamkulu amamva bwanji mtumiki wake akasiya kumutumikira? Yesu anafotokoza mmene Yehova amamvera pamene anafunsa ophunzira ake kuti: “Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo? Akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasochera zija.”—Mat. 18:12, 13. w20.06 19-20 ¶8-9
Lachisanu, July 8
Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino.—1 Tim. 3:1.
Timaona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira Yehova m’njira iliyonse imene tingathe. (Sal. 27:4; 84:10) Ngati m’bale ali ndi mtima wofuna kuchita zambiri potumikira Yehova, ndiye kuti akuchita bwino. Koma m’bale akapatsidwa udindo winawake, sayenera kuyamba kudziganizira kwambiri kuposa mmene ayenera kudziganizira. (Luka 17:7-10) Ayenera kukhala ndi cholinga chotumikira ena modzichepetsa. (2 Akor. 12:15) Baibulo limanena za anthu amene ankadziganizira kwambiri kuposa mmene ankayenera kudziganizira. Mmodzi mwa anthuwa ndi Diotirefe, yemwe sanasonyeze mtima wodzichepetsa koma ankakonda kukhala “woyamba” mumpingo. (3 Yoh. 9) Wina ndi Uziya, yemwe chifukwa cha kunyada anagwira ntchito imene sankayenera kugwira. (2 Mbiri 26:16-21) Winanso ndi Abisalomu, yemwe ankanamizira kuti amakonda anthu pofuna kuwakopa kuti amuthandize kukhala mfumu. (2 Sam. 15:2-6) Zitsanzo za m’Baibulozi zikusonyeza kuti Yehova sasangalala ndi anthu amene amadzifunira ulemerero. (Miy. 25:27) M’kupita kwa nthawi anthu onyada komanso amene amafuna kuti anthu ena aziwalemekeza, amapeza mavuto.—Miy. 16:18. w20.07 4 ¶7-8
Loweruka, July 9
Pakuti aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Mabanja ena a Chikhristu asamukira kumayiko ena chifukwa cha mavuto omwe ali m’mayiko awo kapena kuti akapeze ntchito. Zikatere, ana awo akamapita kusukulu angaphunzire chinenero cha m’dziko lomwe asamukiralo. Makolo nawonso angafunike kuphunzira chinenero cha m’dzikolo kuti apeze ntchito. Koma bwanji ngati m’deralo muli mpingo kapena kagulu kachinenero chakwawo? Kodi banjali liyenera kumasonkhana mpingo wachinenero chiti, cha m’dzikolo kapena chakwawo? Mutu wabanja uyenera kusankha mpingo umene banja lake lizisonkhana. Komabe, ayenera kusankha zinthu zomwe zingathandizedi banjalo. Popeza aliyense ali ndi ufulu wosankha pankhaniyi, tiyenera kulemekeza zimene mutu wabanjalo wasankha. Ngati mutu wabanja wasankha kuti azisonkhana ndi mpingo wathu, tiyenera kuwalandira ndi manja awiri n’kumasonyeza kuti timawakonda.—Aroma 15:7. w20.08 30 ¶17-18
Lamlungu, July 10
Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko.—1 Akor. 1:27.
Ngati tikufuna kuti Yehova azitipatsa mphamvu, sitiyenera kuganiza kuti thanzi, maphunziro, chikhalidwe komanso chuma chimene tili nacho n’zimene zimachititsa kuti tikhale ofunika. Zinthu zimenezi sizichititsa munthu kukhala wofunika kwa Yehova. Ndipotu pakati pa anthu a Mulungu si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru, amphamvu komanso si ambiri omwe ali ochokera m’mabanja achifumu. (1 Akor. 1:26) Choncho simuyenera kudziona kuti simungatumikire Yehova chifukwa choti mulibe zinthu zinazake. Koma muziona kuti zimenezi zingakupatseni mwayi woona mmene Yehova akukuthandizirani pokupatsani mphamvu. Mwachitsanzo, ngati mumachita mantha ndi anthu amene amatsutsa zimene mumakhulupirira, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti muzitha kuuza ena zimene mumakhulupirira. (Aef. 6:19, 20) Kapena ngati mukudwala matenda aakulu omwe amakulepheretsani kuchita zinthu zina, muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu zimene zingakuthandizeni kuti muzimutumikira nthawi zonse. Mukaona kuti Yehova akukuthandizani, chikhulupiriro chanu chimalimba ndipo mumakhala amphamvu. w20.07 16 ¶9
Lolemba, July 11
Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.—Mat. 6:33.
Kuti tiike mzinda wa Mulungu kapena kuti Ufumu pamalo oyamba ngati mmene Abulahamu anachitira, tiyenera kulolera kusiya zinthu zina kuti tisangalatse Mulungu. (Maliko 10:28-30; Aheb. 11:8-10) Tisamaganize kuti sitizikumana ndi mavuto. Chifukwa ngakhale anthu amene adzipereka kutumikira Yehova kwa moyo wawo wonse amakumananso ndi mavuto. (Yak. 1:2; 1 Pet. 5:9) Masiku ano, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuganizira zam’tsogolo. Zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli zikusonyeza kuti panopo tili kumapeto kwa masiku otsiriza. Pali madalitso ambiri amene tidzasangalale nawo mu Ufumu wa Mulungu. Limodzi mwa madalitsowa ndi loti anzathu komanso achibale athu amene anamwalira adzaukitsidwa. Pa nthawiyi, Yehova adzadalitsa Abulahamu chifukwa cha kukhulupirika komanso kuleza mtima kwake, pomuukitsa limodzi ndi banja lake. Kodi inuyo mudzapezekapo kuti mudzawalandire? Zimenezi zingadzatheke ngati nanunso, mofanana ndi Abulahamu, mumalolera kudzimana zinthu zina chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, ngati mumakhulupirirabe Mulungu ngakhale mukumane ndi mavuto komanso ngati mumayembekezera moleza mtima malonjezo a Yehova.—Mika 7:7. w20.08 5-6 ¶13-14; 7 ¶17
Lachiwiri, July 12
Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.—Chiv. 2:10.
Timadziwa kuti ngati adani athu angatiphe, Yehova adzatiukitsa. Timadziwanso kuti palibe chomwe iwo angachite chimene chingatilepheretse kutumikira Yehova. (Aroma 8:35-39) Apatu Yehova anasonyeza kuti ndi wanzeru kwambiri potipatsa chiyembekezo chakuti akufa adzaukitsidwa. Chiyembekezochi chimatithandiza kuti tisamachite mantha adani athu akamatiopseza kuti atipha tikapanda kuchita zimene akufuna. Chimatithandizanso kukhala olimba mtima ndiponso okhulupirika kwa Yehova. Ngati adani a Yehova akukuopsezani kuti akuphani, kodi mudzakhulupirira kuti iye adzakuukitsani? Kodi mungadziwe bwanji ngati mungadzakhulupirire Yehova pa nthawiyo? Njira ina ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimasankha tsiku lililonse zimasonyeza kuti ndimakhulupirira Yehova?’ (Luka 16:10) Funso lina lingakhale lakuti, ‘Kodi mmene ndimachitira zinthu pa moyo wanga ndimasonyeza kuti ndimakhulupirira lonjezo la Yehova loti adzandisamalira ndikamaika zinthu za Ufumu pamalo oyamba?’ (Mat. 6:31-33) Ngati mwayankha kuti “inde” pa mafunso onsewa, ndiye kuti mumakhulupirira Yehova ndipo ndinu okonzeka kulimbana ndi mayesero aliwonse omwe mungadzakumane nawo.—Miy. 3:5, 6. w20.08 17-18 ¶15-16
Lachitatu, July 13
Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi ndi ntchito imene wagwira, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.—2 Tim. 2:15.
Timafunika kukhala aluso tikamagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Tingaphunzire ena mwa malusowa pamisonkhano yathu. Koma kuti tithandize ena kukhulupirira kuti mfundo za m’Baibulo zingawathandize, tiyenera kumaliphunzira nthawi zonse. Tiyenera kumagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu polimbitsa chikhulupiriro chathu. Kuchita zimenezi kumafuna zambiri osati kungowerenga Baibulo. Kumafuna kuti tiziganizira mozama zimene tikuwerenga komanso kufufuza m’mabuku athu kuti tizimvetsa molondola Malemba n’kumawagwiritsa ntchito pa moyo wathu. (1 Tim. 4:13-15) Tikatero m’pamene tingakwanitse kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa ena. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuchita zambiri osati kungowawerengera mavesi a m’Baibulo. Tiyenera kuthandiza anthuwo kumvetsa mavesiwo komanso mmene angawagwiritsire ntchito. Tikamayesetsa kuphunzira Baibulo patokha nthawi zonse, tikhoza kumagwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu pophunzitsa ena.—2 Tim. 3:16, 17. w20.09 28 ¶12
Lachinayi, July 14
Ganizirani mozama [za Yesu] . . . , kuti musatope ndiponso kuti musalefuke.—Aheb. 12:3.
Kuganizira mmene Yehova amatithandizira tikamagwira ntchitoyi, kungatithandize kuti tiziiona kuti ndi yofunika kwambiri. Mwachitsanzo, amatipatsa chakudya chauzimu chochuluka kwambiri kudzera m’mabuku, zinthu zongomvetsera, m’mavidiyo komanso webusaiti yathu. Tangoganizani, pofika pano webusaiti yathu ili m’zinenero zoposa 1,000. (Mat. 24:45-47) Chinthu china chomwe chingatithandize kuti tiziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri, ndi kutengera chitsanzo cha Yesu. Iye sankalola kusokonezedwa ndi chilichonse akamagwira ntchito yolalikira. (Yoh. 18:37) Sanakopeke pamene Satana “anamuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo”, komanso anakana pamene anthu ena ankafuna kumuveka ufumu. (Mat. 4:8, 9; Yoh. 6:15) Yesu sanalole kuti mtima wokonda chuma umusokoneze komanso sanasiye kulalikira, ngakhale anthu ena ankamutsutsa kwambiri. (Luka 9:58; Yoh. 8:59) Ngati titatsatira malangizo a mtumwi Paulo amene ali mulemba lalerowa pamene tikukumana ndi mayesero, tingapitirizebe kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika. w20.09 9-10 ¶6-7
Lachisanu, July 15
Muzitsanzira ine, monga mmene inenso ndimatsanzirira Khristu.—1 Akor. 11:1.
Timasangalala kuti tili ndi alongo ambiri mumpingo omwe amagwira ntchito mwakhama. Iwo amayankha komanso kukamba nkhani pamisonkhano, ndiponso amagwira nawo ntchito yolalikira. Ena amathandiza nawo ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu, komanso amasonyeza kuti amaganizira abale ndi alongo awo. Komabe alongowa amakumananso ndi mavuto. Ena amasamalira makolo awo okalamba. Ena amatsutsidwa ndi achibale awo. Komanso ena amalera okha ana ndipo amafunika kuti agwire ntchito mwakhama kuti asamalire banja lawo. N’chifukwa chiyani tiyenera kumalimbikitsa alongo mumpingo? Tiyenera kuchita zimenezi chifukwa anthu m’dzikoli salemekeza akazi. Komanso Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziwathandiza. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauza Akhristu a mumpingo wa Roma kuti alandire mlongo Febe komanso “kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo.” (Aroma 16:1, 2) Paulo anali wachikhalidwe chimene anthu ake ankaona kuti akazi ndi otsika ndipo sankawalemekeza. Koma atakhala Mkhristu ankatsanzira Yesu, ndipo ankalemekeza akazi komanso kumachita nawo zinthu mokoma mtima. w20.09 20 ¶1-2
Loweruka, July 16
Mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.—Mat. 28:19, 20.
Kuti tithandize ophunzira Baibulo kuti azifunitsitsa kugwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino, tingawafunse mafunso ngati awa: “Kodi moyo wanu wasintha bwanji chifukwa chotsatira mfundo zimene mukuphunzira m’Baibulo? Kodi mukuganiza kuti pali anthu enanso omwe akufunika kumva mfundo za m’Baibulozi? Ndiye kodi mungachite chiyani kuti muwathandize?” (Miy. 3:27; Mat. 9:37, 38) Kumbukirani kuti Yesu anatilangiza kuti tiziphunzitsa ena kuti ‘azisunga zinthu zonse’ zimene analamula. N’zosachita kufunsa kuti zinthu zimenezi zikuphatikizapo malamulo awiri akuluakulu, omwe ndi akuti tizikonda Mulungu komanso tizikonda anzathu. Malamulo awiri onsewa akugwirizana ndi ntchito yathu yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mat. 22:37-39) Ndipotu chikondi ndi chimene chimatichititsa kuti tizilalikira. N’zoona kuti ophunzira Baibulo ena amachita mantha akaganizira za ntchito yolalikira. Koma tiyenera kuwatsimikizira kuti Yehova adzawathandiza ndipo pang’ono ndi pang’ono adzasiya kuopa anthu.—Sal. 18:1-3; Miy. 29:25. w20.11 3 ¶6-8
Lamlungu, July 17
Sitinaleke kukupemphererani.—Akol. 1:9.
Mukamakonzekera phunziro la Baibulo, muzipemphera kwa Yehova ndipo m’pempherolo muzitchula wophunzira wanuyo komanso zosowa zake. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti muziphunzitsa mfundo za m’Baibulo m’njira yakuti zimufike munthuyo pamtima. Muzikumbukira kuti cholinga chanu n’choti mumuthandize mpaka afike pobatizidwa. ophunzira Baibulo angamapindulenso ngati atamachita zinthu zina paokha tsiku lililonse. Ayenera kumalankhulana ndi Yehova. Kodi angachite bwanji zimenezi? Angachite zimenezi akamamvetsera komanso kulankhula ndi Yehova. Angamvetsere kwa Mulungu, akamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Yos. 1:8; Sal. 1:1-3) Muzilimbikitsa wophunzira wanu kuti azilankhula ndi Yehova popemphera tsiku lililonse. Muzipemphera mochokera pansi pamtima ndi wophunzira wanu musanayambe komanso mukamaliza kuphunzira ndipo muzimutchula m’mapempherowo. Wophunzirayo angaphunzire kupemphera kuchokera mumtima akamamvetsera mmene inuyo mumapempherera ndipo nayenso akhoza kumapemphera kwa Yehova Mulungu, m’dzina la Yesu Khristu. (Mat. 6:9; Yoh. 15:16) Wophunzira Baibulo akamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, komwe ndi (kumvetsera kwa Yehova) komanso kupemphera komwe ndi (kulankhula ndi Yehova) adzakhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu.—Yak. 4:8. w20.10 8 ¶8; 9 ¶10-11
Lolemba, July 18
Kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. . . . mothandizidwa ndi mzimu woyera.—Aef. 4:3.
Masiku anonso, gulu la Yehova limathandiza Akhristu m’mipingo yonse kuti azichita zinthu mwadongosolo komanso kuti azikhala mwamtendere ngati mmene Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachitira. (Mac. 16:4, 5) Mwachitsanzo ngati mukupita kukasonkhana kumpingo wina kaya wa dziko lina kapena m’dziko lanu lomwelo, mumadziwa mmene Phunziro la Nsanja ya Olonda likachitidwire komanso mutu umene mukaphunzire. Choncho mukafika kumisonkhanoko simuchitanso chilendo. Ndi mzimu wa Mulungu wokha umene umachititsa kuti atumiki a Mulungu azitumikira mogwirizana padziko lonse. (Zef. 3:9) Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere mumpingo? Kodi ndimamvera amene amatitsogolera? Ngati ndili ndi udindo mumpingo, kodi anthu ena amatha kundidalira? Kodi ndimasunga nthawi komanso ndine wokonzeka kuthandiza ndi kutumikira ena?’ (Yak. 3:17) Ngati mukuona kuti pali zina zimene mukufunika kusintha, muzipempha Mulungu kuti akuthandizeni ndi mzimu wake woyera. Mukamalola kuti mzimu woyera ukuthandizeni kusintha makhalidwe komanso zochita zanu, abale ndi alongo angayambe kukukondani komanso kuyamikira zimene mumachita mumpingo. w20.10 23 ¶12-13
Lachiwiri, July 19
Muzichita zimene mawu amanena, osati kungomva chabe.—Yak. 1:22.
Mawu a Mulungu angakhale ngati galasi lathu. (Yak. 1:23-25) Ambirife timadziyang’anira pagalasi m’mawa uliwonse tisanachoke panyumba. Zimenezi zimatithandiza kuti tikonze pofunika kukonza anthu ena asanaone. Mofanana ndi zimenezi, tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse zidzatithandiza kusintha mmene timaganizira komanso mmene timaonera zinthu. Ambiri amaona kuti n’zothandiza kuwerenga lemba latsiku m’mawa uliwonse asanachoke panyumba. Amalola kuti zimene awerengazo zizikhudza mmene amaganizira. Ndiyeno tsiku lonse, amayesetsa kupeza njira zimene angagwiritsire ntchito malangizo a m’Mawu a Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, tsiku lililonse tiyenera kukhala ndi chizolowezi chophunzira, zomwe zikuphatikizapo kuwerenga komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu. Zimenezi zingaoneke ngati zosavuta koma n’zofunika kwambiri kuti tipitirize kuyenda panjira yopanikiza yopita ku moyo. Pamenepa, Mawu a Mulungu tingawayerekezere ndi mashini a X-ray, omwe amatithandiza kuona zinthu zamkati zimene sitikanatha kuziona. Koma tiyenera kukhala odzichepetsa kuti titsatire malangizo ochokera m’Baibulo kapena omwe Akhristu anzathu angatipatse. w20.11 18 ¶3; 20 ¶8
Lachitatu, July 20
Mipingo inapitiriza kulimba m’chikhulupiriro ndipo chiwerengero chinapitiriza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.—Mac. 16:5.
Ngakhale kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankazunzidwa, nthawi zina ankakhala pa mtendere. Ndiye kodi ankatani pa nthawi ya mtendereyi? Amuna ndi akazi okhulupirikawa ankalalikira uthenga wabwino mwakhama. Baibulo limanena kuti anthu amenewa ‘ankayenda moopa Yehova.’ Iwo anapitirizabe kulalikira uthenga wabwino, ndipo zotsatira zake zinali zakuti mpingowo unapitirizabe “kukulirakulira.” N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa khama limene anasonyeza pa nthawi ya mtendereyi. (Mac. 9:26-31) Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankagwiritsa ntchito mwayi uliwonse kuti azilalikira uthenga wabwino. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ataona kuti angalalikire kwa anthu ambiri ku Efeso, anakhalabe mumzindawo n’kumalalikira. (1 Akor. 16:8, 9) Anthu onse m’mipingo anayamba kulalikira mwakhama “uthenga wabwino wa mawu a Yehova.” (Mac. 15:30-35) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Zotsatira zake ndi zimene lemba laleroli likunena. w20.09 16 ¶6-8
Lachinayi, July 21
Imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi.—1 Akor. 15:21.
Adamu atachimwa anabweretsa mavuto pa iyeyo ndi ana ake onse. Panopa tikupitiriza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha kusamvera kwake. Koma popeza kuti Mulungu anaukitsa mwana wake, tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. “Kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi,” yemwe ndi Yesu. Mtumwi Paulo ananenanso kuti: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akor. 15:22) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti “mwa Adamu onse akufa”? Paulo ankanena za anthu onse amene anatengera uchimo kuchokera kwa Adamu ndipo amafa. (Aroma 5:12) Adamu sali m’gulu la anthu amene ‘adzapatsidwe moyo.’ Iye sangapindule ndi nsembe ya Khristu chifukwa anali wangwiro koma anasankha dala kuti asamvere Mulungu. Zimene zinachitikira Adamu ndi zomwe zidzachitikirenso anthu amene “Mwana wa munthu” adzawaweruze kuti ndi “mbuzi,” kutanthauza kuti adzapita ku “chiwonongeko chotheratu.”—Mat. 25:31-33, 46; Aheb. 5:9. w20.12 5 ¶13-14
Lachisanu, July 22
Yehova . . . amaona wodzichepetsa.—Sal. 138:6.
Ngati sitinapatsidwe utumiki wina wake, tiziganizira chitsanzo cha angelo okhulupirika. Mwachitsanzo nthawi ina Yehova anafunsa angelo kuti apereke maganizo awo pa mmene angapusitsire Mfumu Ahabu yemwe anali woipa. Angelo angapo anapereka maganizo awo. Koma Mulungu anasankha mngelo mmodzi n’kumuuza kuti maganizo ake ndi omwe angathandize. (1 Maf. 22:19-22) Kodi angelo ena okhulupirikawo anafooka n’kumaganiza kuti, ‘Ndangotaya nthawi kupereka maganizo anga?’ Ayi sichoncho. Tikutero chifukwa angelo ndi odzichepetsa kwambiri ndipo amafuna kuti ulemerero wonse uzipita kwa Yehova. (Ower. 13:16-18; Chiv. 19:10) Tizikumbukira kuti tili ndi mwayi wodziwika ndi dzina la Mulungu komanso wolalikira za Ufumu wake. Utumiki umene timachita si umene umapangitsa kuti tikhale amtengo wapatali kwa Mulungu. Chimene chingachititse kuti tikhale amtengo wapatali kwa Yehova komanso kwa abale ndi alongo athu ndi kudzichepetsa. Ndiye tizipempha Yehova kuti atithandize kukhalabe odzichepetsa. Tiziganizira zitsanzo za atumiki odzichepetsa a Yehova zopezeka m’Baibulo. Tizikhala ofunitsitsa kutumikira abale athu mmene tingathere.—1 Pet. 5:5. w20.12 26 ¶16-17
Loweruka, July 23
Landirani chisoti cholimba chachipulumutso, ndiponso lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu.—Aef. 6:17.
Chisoti chachipulumutso chikuimira chiyembekezo chimene Yehova watipatsa choti adzatipulumutsa ku imfa komanso adzapereka mphoto kwa onse amene amachita chifuniro chake. (1 Ates. 5:8; 1 Tim. 4:10; Tito 1:1, 2) Chiyembekezo chathu chachipulumutso chimateteza maganizo athu. Chimatithandiza kuti tiziganizira zomwe Mulungu walonjeza komanso kuti tiziona moyenera mavuto omwe timakumana nawo. Timavala chisoti chimenechi tikamaganiza mogwirizana ndi zomwe Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, sitimadalira chuma chosadalirika koma timadalira Mulungu. (Sal. 26:2; 104:34; 1 Tim. 6:17) Lupanga la mzimu ndi Mawu a Mulungu, Baibulo. Lupangali lili ndi mphamvu yothetsa chinyengo komanso kumasula anthu ku ziphunzitso zabodza ndi makhalidwe oipa. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 4:12) Timaphunzira mmene tingagwiritsire ntchito lupangali moyenera tikamaphunzira patokha komanso kudzera m’maphunziro amene gulu la Mulungu limatipatsa.—2 Tim. 2:15. w21.03 27 ¶4; 29 ¶10-11
Lamlungu, July 24
Ine . . . ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.—Chiv. 1:9.
Ngakhale kuti anamangidwa chifukwa cholalikira za Yesu, mtumwi Yohane anasonyeza kuti ankakonda anthu ena. Mwachitsanzo, iye analemba buku la Chivumbulutso n’kulitumiza kumipingo n’cholinga choti Akhristu anzake adziwe ‘zinthu zimene zimayenera kuchitika posachedwapa.’ (Chiv. 1:1) Kenako Yohane analemba Uthenga Wabwino wonena za moyo wa Yesu ndi utumiki wake. Pa nthawiyi ayenera kuti anali atatulutsidwa m’ndende pachilumba cha Patimo. Iye analembanso makalata atatu n’cholinga chofuna kulimbikitsa abale ndi alongo ake. Tiyenera kutsanzira Yohane yemwe anasonyeza kuti anali ndi moyo wodzimana komanso tizisonyeza kuti timakonda anthu ena ndi zimene timasankha kuchita pa moyo wathu. Dziko la Satanali limafuna kuti tizithera nthawi yathu komanso mphamvu zathu zonse pochita zofuna zathu zokha monga ngati kufunafuna ndalama kapena kutchuka. Koma Akhristu padziko lonse, amasonyeza mtima wodzimana ndipo amathera nthawi yawo yambiri polalikira uthenga wabwino komanso kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. w21.01 10 ¶9-10
Lolemba, July 25
[Yonatani] anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.—1 Sam. 18:1.
Yonatani akanatha kuchitira nsanje Davide. Monga mwana wa Mfumu Sauli, iye akanatha kuganiza kuti ndiye anali woyenerera kukhala mfumu m’malo mwa bambo ake. (1 Sam. 20:31) Koma Yonatani anali wodzichepetsa ndipo anali wokhulupirika kwa Yehova. Iye anagwirizana kwambiri ndi zimene Yehova anasankha kuti Davide adzakhale mfumu. Komanso iye anali wokhulupirika kwa Davide ngakhale kuti zimenezi zinakwiyitsa kwambiri bambo ake Sauli. (1 Sam. 20:32-34) Yonatani ankakonda kwambiri Davide ndipo sankamuchitira nsanje. Iye anali katswiri woponya mivi komanso msilikali wolimba mtima. Yonatani ndi bambo ake Sauli ankadziwika kuti “anali aliwiro kuposa chiwombankhanga” komanso “amphamvu kuposa mikango.” (2 Sam. 1:22, 23) Choncho Yonatani akanatha kumadzikweza chifukwa cha luso limene anali nalo. Komabe Yonatani sankachita zinthu mwampikisano kapena kuchita nsanje chifukwa cha zabwino zimene Davide anachita. M’malomwake iye ankasirira kulimba mtima kwa Davide komanso kudalira kwake Yehova. Ndipotu panali pambuyo poti Davide wapha Goliati pamene Yonatani anayamba kumukonda kwambiri. w21.01 21 ¶6; 22 ¶8-9
Lachiwiri, July 26
Mutu wa mkazi ndi mwamuna.—1 Akor. 11:3.
Akhristu onse amatsogoleredwa ndi Yesu yemwe ndi wangwiro. Komabe mkazi wa Chikhristu akakwatiwa, amatsogoleredwa ndi mwamuna yemwe si wangwiro. Zimenezitu sizikhala zophweka nthawi zonse. Choncho akamaganizira za mwamuna yemwe akufuna kudzakhala naye pabanja, mkazi angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘N’chiyani chikusonyeza kuti m’baleyu adzakhala mutu wa banja wabwino? Kodi amaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri pa moyo wake? Ngati si choncho, n’chiyani chikundipangitsa kuganiza kuti iye adzathandiza banja lathu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?’ Mlongoyo angachitenso bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndili ndi makhalidwe ati amene angathandize kuti ndidzakhale ndi banja labwino? Kodi ndine woleza mtima komanso wopatsa? Kodi ndili pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?’ (Mlal. 4:9, 12) Zimene mkazi angasankhe asanakwatiwe, zingachititse kuti adzakhale ndi banja labwino komanso losangalala. Alongo ambiri a Chikhristu ndi zitsanzo zabwino pa nkhani yogonjera amuna awo. Timawayamikira kwambiri chifukwa cha zimenezi. w21.02 8 ¶1-2
Lachitatu, July 27
Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.—Mac. 16:9.
Zaka zapitazi, ofalitsa ambiri akhala akuphunzira zinenero zina kuti awonjezere utumiki wawo. Kuti achite zimenezi, amafunika kusintha zinthu zina pa moyo wawo. Abale ndi alongowa ankafunika kusiya mpingo wachinenero chawo n’kusamukira mumpingo wachinenero china komanso kumene kukufunika ofalitsa ambiri. Mkhristu aliyense amasankha yekha kuchita zimenezi n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova. Ngakhale kuti pamatenga zaka kuti adziwe bwino chinenero chatsopanocho, iwo amathandiza kwambiri mpingo umene asamukirawo. Amalimbikitsa mpingo chifukwa cha zimene akudziwa komanso makhalidwe awo abwino. Timaona abale ndi alongo odziperekawa kuti ndi amtengo wapatali. Bungwe la akulu siliyenera kulephera kuika m’bale kuti atumikire monga mkulu kapena mtumiki wothandiza chifukwa choti amavutika kulankhula chinenero cha mpingowo. Akulu ayenera kugwiritsa ntchito Malemba kuti aone ngati m’baleyo akuyenerera kutumikira monga mkulu kapena mtumiki wothandiza, osati potengera mmene amalankhulira chinenerocho.—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9. w20.08 30 ¶15-16
Lachinayi, July 28
Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana.—Yak. 1:2.
Anthu ambiri amaganiza kuti angakhale osangalala ngati ali ndi thanzi labwino, ndalama zambiri komanso banja losangalala. Komatu chimwemwe chimene Yakobo ankanena ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa ndipo sichidalira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthu. (Agal. 5:22) Mkhristu angakhale ndi chimwemwe kapena kuti wosangalala, akadziwa kuti akusangalatsa Yehova komanso kutsatira chitsanzo cha Yesu. (Luka 6:22, 23; Akol. 1:10, 11) Chimwemwe chimene chimakhala mumtima mwa Mkhristu chili ngati lawi la nyale yagalasi lomwe limakhala lotetezeka. Lawilo limayakabe ngakhale kukuomba mphepo kapena kukugwa mvula. Chimwemwe chimenechi chimakhalapobe ngakhale tidwale kapena tikhale ndi ndalama zochepa. Ndipo sichitha ngakhale pamene anthu ena kapena a m’banja lathu akutinyoza kapena kutitsutsa. M’malo mokhala okhumudwa, chimwemwe chathu chimawonjezereka nthawi iliyonse imene anthu ena akufuna kutilanda chimwemwecho. Mayesero amene timakumana nawo chifukwa cha chikhulupiriro chathu ndi amene amatsimikizira kuti ndifedi ophunzira a Khristu. (Mat. 10:22; 24:9; Yoh. 15:20) N’chifukwa chake Yakobo analemba zimene zili m’lemba laleroli. w21.02 28 ¶6
Lachisanu, July 29
Mawu abwino ndi amene amausangalatsa [mtima].—Miy. 12:25.
Mukamawerenga Baibulo n’kupeza mavesi amene akusonyeza kuti mungapeze mphamvu chifukwa chodalira Yehova, muziyesa kuloweza mavesi amenewo. Kuti muloweze muziwawerenga motulutsa mawu kapena kuwalemba penapake n’kumawawerenga mobwerezabwereza. Yoswa analamulidwa kuwerenga komanso kuganizira zimene zinali m’buku la Chilamulo n’cholinga choti azichita zinthu mwanzeru. Zimene akanawerenga zikanamuthandiza kuti asamachite mantha koma azichita zinthu molimba mtima potsogolera anthu a Mulungu. (Yos. 1:8, 9) Inunso zimene mungawerenge m’Mawu a Mulungu zingakuthandizeni kukhala ndi mtendere wam’maganizo ngakhale pa nthawi imene mwakumana ndi zinthu zomwe zikanachititsa kuti muzida nkhawa kapena kuchita mantha. (Sal. 27:1-3; Miy. 3:25, 26) Tikakhala pamisonkhano timapindula ndi malangizo a munkhani zimene abale amakamba, ndemanga zimene abale ndi alongo amapereka komanso nkhani zolimbikitsa zimene timacheza ndi abale ndi alongo athu. (Aheb. 10:24, 25) Timalimbikitsidwanso kwambiri tikamafotokozera anzathu a mumpingo zinthu zimene zikutidetsa nkhawa. w21.01 6 ¶15-16
Loweruka, July 30
Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika.—1 Tim. 4:12.
Pamene munabatizidwa, munasonyeza kuti mumadalira Yehova komanso kumukhulupirira kwambiri. Ndipo iye anasangalala n’kukupatsani mwayi wokhala m’banja lake. Panopa chimene muyenera kuchita ndi kupitirizabe kumudalira. Zingakhale zosavuta kudalira Yehova mukamafuna kusankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri pa moyo wanu, koma nanga bwanji pa nkhani zing’onozing’ono? N’zofunika kwambiri kuti muzidalira Yehova mukamasankha zochita pa nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo zosangalatsa, ntchito komanso zolinga zimene muli nazo pa moyo wanu. Musamadalire nzeru zanu. M’malomwake muzifufuza mfundo za m’Baibulo zokhudza zimene mukufuna kusankha ndipo muzichita zinthu mogwirizana ndi malangizowo. (Miy. 3:5, 6) Mukamachita zimenezi mudzasangalatsa mtima wa Yehova ndipo anthu ena mumpingo adzayamba kukulemekezani. N’zoona kuti inunso achinyamata mofanana ndi aliyense, si inu angwiro ndipo mumalakwitsa zinthu zina. Komabe zimenezi siziyenera kukulepheretsani kuchita zonse zimene mungathe potumikira Yehova. w21.03 6 ¶14-15
Lamlungu, July 31
Ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.—2 Tim. 4:17.
Kodi anthu a m’banja lanu amakutsutsani chifukwa choti mukutumikira Yehova? Kapena kodi mukukhala m’dziko limene ntchito ya Mboni za Yehova ndi yoletsedwa? Ngati ndi choncho mungalimbikitsidwe mutawerenga lemba la 2 Timoteyo 1:12-16 ndi 4:6-11, 17-22. Mtumwi Paulo analemba mavesi a m’Baibulo amenewa ali m’ndende. Musanawerenge mavesiwa, muuzeni Yehova vuto limene mwakumana nalo komanso muzimufotokozera mmene mukumvera. Kenako muzimupempha kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene zingakuthandizeni polimbana ndi vuto lanu. Yehova anali atamuchenjezeratu Paulo kuti adzazunzidwa chifukwa chokhala Mkhristu. (Mac. 21:11-13) Koma kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Anayankha mapemphero ake ndipo anamupatsa mphamvu. Paulo anauzidwa kuti adzapatsidwa mphoto imene anaigwirira ntchito mwakhama kuti aipeze. Kuwonjezera pamenepo, Yehova anachititsa anzake okhulupirika kuti amuthandize. w21.03 17-18 ¶14-15, 19