Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es22 tsamba 77-87
  • August

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • August
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
  • Timitu
  • Lolemba, August 1
  • Lachiwiri, August 2
  • Lachitatu, August 3
  • Lachinayi, August 4
  • Lachisanu, August 5
  • Loweruka, August 6
  • Lamlungu, August 7
  • Lolemba, August 8
  • Lachiwiri, August 9
  • Lachitatu, August 10
  • Lachinayi, August 11
  • Lachisanu, August 12
  • Loweruka, August 13
  • Lamlungu, August 14
  • Lolemba, August 15
  • Lachiwiri, August 16
  • Lachitatu, August 17
  • Lachinayi, August 18
  • Lachisanu, August 19
  • Loweruka, August 20
  • Lamlungu, August 21
  • Lolemba, August 22
  • Lachiwiri, August 23
  • Lachitatu, August 24
  • Lachinayi, August 25
  • Lachisanu, August 26
  • Loweruka, August 27
  • Lamlungu, August 28
  • Lolemba, August 29
  • Lachiwiri, August 30
  • Lachitatu, August 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
es22 tsamba 77-87

August

Lolemba, August 1

Simungathe kuchita kalikonse popanda ine.​—Yoh. 15:5.

Anzake apamtima a Yesu ndi okhawo amene amathandizidwa ndi nsembe yake ya dipo. Yesu ananena kuti adzapereka “moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Anthu okhulupirika amene anakhala moyo Yesu asanabwere padzikoli adzafunika kuphunzira za iye komanso kumukonda. N’zoona kuti anthu monga Abulahamu, Sara, Mose ndi Rahabi adzaukitsidwa. Koma kuti adzapeze moyo wosatha, adzayenera kudziwa za Yesu komanso kukhala anzake. (Yoh. 17:3; Mac. 24:15; Aheb. 11:8-12, 24-26, 31) Timasangalala kugwira ntchito ndi Yesu polalikira komanso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu. Yesu ali padzikoli anali mphunzitsi. Atabwerera kumwamba, iye anakhala mutu wa mpingo ndipo akupitiriza kutsogolera pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Yesu amaona komanso kuyamikira zimene mumachita poyesetsa kuthandiza anthu kuti amudziwe iyeyo ndiponso Atate wake. Sitingakwanitse kugwira bwino ntchito imeneyi popanda kuthandizidwa ndi Yehova komanso Yesu.​—Yohane 15:4. w20.04 22 ¶7-8

Lachiwiri, August 2

Mafumu awiri amenewa . . . azidzalankhula bodza patebulo limodzi.—Dan. 11:27.

Mawu akuti “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwera” ankanena za maboma amphamvu omwe anali kumpoto komanso kum’mwera kwa dziko la Isiraeli. (Dan. 10:14) Mtundu wakale wa Isiraeli ndi umene unali anthu a Mulungu mpaka pa Pentekosite mu 33 C.E. Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova anasonyeza bwino kuti ophunzira okhulupirika a Yesu ndi amene anali anthu ake. Choncho mbali yaikulu ya ulosi wa mu Danieli chaputala 11 imanena zokhudza otsatira a Khristu osati mtundu wakale wa Isiraeli. (Mac. 2:1-4; Aroma 9:6-8; Agal. 6:15, 16) Mayiko omwe anali mfumu ya kumpoto komanso mfumu yakum’mwera akhala akusintha. Ngakhale zili choncho, zinthu zitatu izi sizinasinthe ndipo zingatithandize kuwadziwa. Choyamba, amalamulira komanso kuzunza anthu a Mulungu. Chachiwiri, zimene amachitira anthu a Mulungu zimasonyeza kuti amadana ndi Yehova. Ndipo chachitatu, amalimbirana ulamuliro. w20.05 3 ¶3-4

Lachitatu, August 3

Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.​—Eks. 3:14.

Yehova amachititsa zinthu kuchitika pokhala chilichonse chimene akufunikira, kuti akwaniritse cholinga chake. (Eks. 3:13, 14) Nthawi zambiri timalimbikitsidwa kuti tiziganizira mfundo yochititsa chidwi imeneyi. Yehova angachititsenso atumiki ake opanda ungwiro kuti akhale chilichonse chimene akufunikira kuti amutumikire komanso kukwaniritsa cholinga chake. (Yes. 64:8) Mwa njira imeneyi, palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa zolinga zake. (Yes. 46:10, 11) Kuganizira mozama zimene Yehova wachita komanso zimene watithandiza kuchita, kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri Atate wathu wakumwambayu. Mwachitsanzo, tikamaganizira za zinthu zodabwitsa zomwe analenga, timagoma kwambiri. (Sal. 8:3, 4) Komanso tikamaganizira zimene Yehova watithandiza kuchita kuti tikwaniritse cholinga chake, timayamba kumulemekeza kwambiri. Kunena zoona dzina la Yehova ndi lochititsa mantha. Tanthauzo lake limatiuza zonse zokhudza mmene Atate wathu alili, zonse zimene anachita komanso zonse zimene adzachite m’tsogolo.​—Sal. 89:7, 8. w20.06 9-10 ¶6-7

Lachinayi, August 4

Mulungu . . . ndi amene amapatsa anthu onse moyo ndi mpweya.—Mac. 17:24, 25.

Anthufe komanso zinyama timafunikira mpweya wa okosijeni kuti tikhale ndi moyo. Akatswiri ena amati pa chaka chimodzi chokha, timapuma mpweya wa okosijeni wokwana matani handiredi biliyoni. Ndiye tikamapuma, timatulutsa mpweya wotchedwa kaboni daiokisaidi. Komabe okosijeni samatha zamoyozi zikamapuma, komanso kaboni daiokisaidi safika pochuluka kwambiri moti n’kudzaza m’mlengalenga monse. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa choti Yehova analenganso zomera monga mitengo ndi zina. Zomerazi zimapuma kaboni daiokisaidi ndi kutulutsa okosijeni. Mpweya womwe timapumawu umapangidwa mwa njira imeneyi. Zimenezi zikutsimikizira mawu opezeka mulemba la lero. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyamikira dziko lathu lokongolali ndi zinthu zonse zomwe zilimo? (Sal. 115:16) Njira imodzi ndi kuganizira mozama zinthu zimene Yehova analenga. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tizimuthokoza tsiku lililonse pa zinthu zabwino zimene amatipatsa. Komanso timasonyeza kuyamikira tikamayesetsa kusamalira malo amene timakhala kuti azikhala aukhondo. w20.05 22 ¶5, 7

Lachisanu, August 5

Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu.​—Ezek. 36:23.

Zimene Yehova wachita pa nkhani yokhudza kuyeretsa dzina lake, zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru, woleza mtima ndiponso wachilungamo. Wasonyezanso mphamvu zake m’njira zambiri. Koposa zonse, wasonyeza kuti ndi Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Yehova akupitirizabe kuyeretsa dzina lake. Masiku ano, Satana akupitirizabe kudetsa dzina la Mulungu. Iye amachititsa kuti anthu azikayikira ngati Mulungu alidi wamphamvu, wachilungamo, wanzeru komanso wachikondi. Mwachitsanzo, amayesetsa kuchititsa anthu kukhulupirira kuti Yehova si Mlengi. Kwa anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu, Satana amawachititsa kuona kuti malamulo a Mulungu si achilungamo ndipo ndi opanikiza. Amaphunzitsanso anthu kuti Mulungu ndi wankhanza ndipo amawotcha anthu. Anthu akakhulupirira mabodza amenewa, kumakhala kosavuta kuti ayambe kukana ulamuliro wolungama wa Yehova. Mpaka pamene adzawonongedwe, Satana apitirizabe kukopa anthu kuti asakhale kumbali ya Mulungu. Koma kodi iye adzapambana? w20.06 5 ¶13-15

Loweruka, August 6

Sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu, koma Khristu ndiye zinthu zonse ndipo ali mwa onse.​—Akol. 3:11.

M’mipingo yambiri mungakhale abale ndi alongo omwe akuyesetsa kuphunzira chinenero chatsopano. Nthawi zina angamavutike kufotokoza maganizo awo. Koma tikamapewa kuganizira kwambiri mmene akuvutikira kulankhula chinenerocho, tingaone kuti amakonda kwambiri Yehova komanso amafuna kumutumikira. Tikamaona makhalidwe awo abwinowa, tingayambe kuwalemekeza komanso kuwaona kuti ndi ofunika kwambiri. Sitikuyenera kumawaona ngati osafunika chifukwa choti amavutika kulankhula chinenero chathu. Kuchita zimenezi kungakhale ngati kuwauza kuti: “Ndilibe nanu ntchito.” (1 Akor. 12:21) Yehova watipatsa ntchito yofunika kwambiri mumpingo wake. Ndiye zilibe kanthu kuti ndife mwamuna kapena mkazi, tili pabanja kapena ayi, ndife wachikulire kapena wachinyamata, timalankhula bwino chinenero chinachake kapena timavutika nacho, tonsefe ndife amtengo wapatali kwa Yehova komanso kwa abale ndi alongo athu. (Aroma 12:4, 5; Akol. 3:10) Choncho tiyeni nthawi zonse tiziyamikira ntchito imene Yehova watipatsa komanso tiziyamikira ntchito imene wapereka kwa abale ndi alongo athu mumpingo wake. w20.08 31 ¶20-22

Lamlungu, August 7

Anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatira a Yesu.—Mac. 17:34.

Mtumwi Paulo sanagwe ulesi pothandiza anthu a ku Atene ngakhale kuti mumzindawu munali mafano ambiri, chiwerewere, nzeru za anthu komanso anthuwo ankamunyoza. Paja Paulo anakhala Mkhristu ngakhale kuti poyamba anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) Yesu anaona kuti Paulo akhoza kukhala wophunzira wake. Ndiyeno Paulo anatsanzira Yesu n’kumaona kuti anthu a ku Atene akhoza kukhala ophunzira. Ndipotu ena mwa anthuwo anakhaladi ophunzira. (Mac. 9:13-15) M’nthawi ya atumwi, anthu osiyanasiyana anakhala ophunzira a Yesu. Polembera Akhristu amumzinda wa Korinto ku Girisi, Paulo ananena kuti anthu ena amumpingowo poyamba ankachita zinthu zoipa kwambiri. Kenako ananena kuti: “Ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera.” (1 Akor. 6:9-11) Mukanakhala inuyo, kodi mukanaona kuti anthu oterewa angasinthe n’kukhala ophunzira? w20.04 12 ¶15-16

Lolemba, August 8

Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga.​—1 Maf. 19:4.

Akulu asamafulumire kuweruza anthu amene ayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kuli kwa phindu. M’malo mowaona ngati anthu oipa, akulu ayenera kumvetsa chimene chikuchititsa anthuwo kulankhula kapena kuchita zinthu mwa njira imeneyo. Kenako ndi pamene angapeze mfundo za m’Malemba zimene angagwiritsire ntchito powalimbikitsa. Mneneri Eliya anathawa, Mfumukazi Yezebeli atamuopseza kuti amupha. (1 Maf. 19:1-3) Iye anaganiza kuti zonse zomwe anachita zinali zopanda phindu. Eliya anapanikizika kwambiri moti analakalaka atangofa. (1 Maf. 19:4, 10) Yehova sanamudzudzule koma anamutsimikizira kuti sanali yekha. Anamulimbikitsa kuti azimudalira chifukwa anali adakali ndi ntchito yambiri yoti agwire. Yehova anamvetsera Eliya moleza mtima komanso anamupatsa utumiki wina. (1 Maf. 19:11-16, 18) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tonsefe, makamaka akulu, tiyenera kuchita zinthu mokoma mtima ndi Akhristu anzathu. Munthu akamafotokoza kuti wakhumudwa ndi zinazake kapena akamakayikira ngati Mulungu angamukhululukiredi, akulu ayenera kumumvetsera moleza mtima. Komanso ayenera kumutsimikizira kuti Yehova amamukonda. w20.06 22 ¶13-14

Lachiwiri, August 9

Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.​—Miy. 17:17.

Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi achibale komanso anzathu. (Sal. 133:1) Yesu anali ndi anzake abwino. (Yoh. 15:15) Baibulo limafotokoza ubwino wokhala ndi anzathu apamtima. (Miy. 18:24) Ndipo limatiuzanso kuti sibwino kudzipatula. (Miy. 18:1) Anthu ambiri amaona kuti kucheza ndi anthu pa intaneti kumawathandiza kupeza anzawo ambiri komanso kuti asamadzimve kuti ali okhaokha. Komabe tiyenera kusamala tikamacheza ndi anthu pogwiritsa ntchito njira imeneyi. Opanga kafukufuku ena anapeza kuti anthu omwe amathera nthawi yaitali akuona zimene ena alemba kapena kuika pa intaneti, akhoza kumadziona kuti ali okhaokha komanso kuyamba kuvutika maganizo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi chingakhale chakuti anthu amakonda kuika zithunzi pa intaneti za zinthu zabwino zimene achita kapena zomwe zawachitikira pa moyo wawo. Zithunzizi zingakhale zawo kapena za anzawo komanso zamalo okongola amene anapitako. Munthu amene amaona zithunzizo akhoza kumaona kuti moyo wake ndi wosasangalatsa poyerekezera ndi wa anzakewo. w20.07 5-6 ¶12-13

Lachitatu, August 10

Atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti akambirane nkhani imeneyi.​—Mac. 15:6.

Nsanja ya Olonda ya October 1, 1988, inanena kuti: “Akulu ayenera kuzindikira kuti Khristu angagwiritse ntchito mzimu woyera pothandiza mkulu aliyense kunena mfundo ya m’Baibulo yomwe ingakhale yothandiza kwambiri posankha zoyenera kuchita. (Mac. 15:7-15) Palibe mkulu winawake amene mzimu woyera ungagwire ntchito kwambiri pa iye kuposa anzake.” Mkulu amene amalemekeza akulu anzake safuna kuti nthawi zonse azingokhala woyambirira kulankhula akamakambirana nkhani inayake. Iye amapewa kulankhula kwambiri ndiponso saona kuti maganizo ake ndi ofunika kuposa a ena. M’malomwake amafotokoza maganizo ake modzichepetsa. Amamvetsera mwatcheru ena akamapereka maganizo awo. Komanso chofunika kwambiri, amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba ndiponso kutsatira malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Akulu akamachita zinthu mwachikondi komanso mwaulemu akakhala pamisonkhano yawo, mzimu woyera umagwira ntchito bwino ndipo umawathandiza kusankha zinthu mwanzeru.​—Yak. 3:17, 18. w20.08 27 ¶5-6

Lachinayi, August 11

Pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.​—Aroma 12:21.

Anthu amene ankadana ndi Paulo anali amphamvu kuposa iyeyo. Nthawi zambiri ankalamula kuti anthu amumenye komanso kumutsekera m’ndende. Paulo ankachitiridwanso zinthu zopanda chilungamo ndi anthu omwe pa nthawi ina anali anzake. Ngakhalenso anthu ena mumpingo wa Chikhristu ankamutsutsa. (2 Akor. 12:11; Afil. 3:18) Koma Paulo anagonjetsa adani ake onse. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye sanasiye kulalikira ngakhale kuti ankamutsutsa. Komanso sanasiye kukonda abale ndi alongo ake ngakhale kuti nthawi zina ankamukhumudwitsa. Koma chofunika kwambiri n’choti Paulo anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kwa moyo wake wonse. (2 Tim. 4:8) Iye anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa sankadalira mphamvu zake koma ankadalira Yehova. Kodi nanunso mumafunika kupirira mukamanyozedwa kapena kuzunzidwa? Cholinga chathu ndi choti tizigonjetsa choipa poyesetsa kuthandiza anthu kuphunzira Mawu a Mulungu. Mungakwanitse cholinga chimenechi mukamagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso a anthu, mukamalemekeza komanso kusonyeza chifundo anthu amene amakuchitirani zoipa ndiponso mukamachitira zabwino anthu onse, ngakhale adani anu.​—Mat. 5:44; 1 Pet. 3:15-17. w20.07 17-18 ¶14-15

Lachisanu, August 12

Kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.​—2 Sam. 22:36.

Kodi n’zomveka kunena kuti Yehova ndi wodzichepetsa? Inde. Umboni wake ndi zimene Davide ananena m’lemba laleroli. (Sal. 18:35) N’kutheka kuti Davide ankaganizira za tsiku limene mneneri Samueli anabwera kunyumba kwa bambo ake kuti adzadzoze munthu yemwe adzakhale mfumu ya Isiraeli. Davide anali wamng’ono kwambiri pa ana aamuna a m’banjalo koma Yehova anamusankha kuti ndi amene adzalowe m’malo mwa Mfumu Sauli. (1 Sam. 16:1, 10-13) Davide anagwirizana ndi zimene wolemba masalimo wina ananena zokhudza Yehova. Wamasalimoyu anati: “Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi. Amakweza munthu wosauka . . . kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka.” (Sal. 113:6-8) Yehova amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa akamachita zinthu ndi anthu ochimwa amene amamulambira. Si kuti iye amangovomereza kuti tizimulambira, koma amationanso ngati anzake. (Sal. 25:14) Kuti tikhale naye pa ubwenzi, Yehova anapereka Mwana wake nsembe kuti machimo athu azikhululukidwa. Izi zikusonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima. w20.08 8 ¶1-3

Loweruka, August 13

Yehova . . . safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.​—2 Pet. 3:9.

Yehova akudziwa tsiku komanso nthawi imene adzawononge dziko loipali. (Mat. 24:36) Iye apitirizabe kuleza mtima mpaka nthawiyo idzakwane. Yehova amafunitsitsa kuukitsa anthu amene anamwalira koma akuleza mtima. (Yobu 14:14, 15) Akudikira kuti nthawi yoyenera yoti adzawaukitse ifike. (Yoh. 5:28) Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova chifukwa cha kuleza mtima kwake. Tangoganizani: Chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova, anthu ambiri kuphatikizapo ifeyo, tinapeza mwayi woti ‘tilape.’ Yehova amafuna kuti anthu ambiri akhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Choncho tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira kuleza mtima kwakeko. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingasonyeze kuyamikira tikamayesetsa kufufuza anthu a ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha,’ n’kuwathandiza kuti ayambe kukonda Yehova komanso kumutumikira. (Mac. 13:48) Tikatero, tidzawathandiza kuti nawonso apindule ndi kuleza mtima kwa Yehova. w20.08 18 ¶17

Lamlungu, August 14

Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova. Ndiphunzitseni kuyenda m’njira zanu.​—Sal. 25:4.

Tiziyesetsa kuti zimene wophunzira wathu akuphunzira m’Baibulo zizimufika pamtima. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa zimene akuphunzirazo zikamamufika pamtima angamazigwiritse ntchito pa moyo wake. Yesu ankaphunzitsa anthu zinthu zambiri ndipo anthuwo ankakonda kumvetsera zimene ankawaphunzitsa. Koma anthu ankamutsatira chifukwa zomwe ankaphunzitsa zinkawafikanso pamtima. (Luka 24:15, 27, 32) Wophunzira wanu ayenera kumaona kuti Yehova ndi weniweni ndipo angathe kukhala naye pa ubwenzi. Azimuona ngati Atate wake, Mulungu wake komanso mnzake. (Sal. 25:5) Kuti zimenezi zitheke, tikamaphunzira naye tizimuthandiza kudziwa makhalidwe abwino a Mulungu wathu. (Eks. 34:5, 6; 1 Pet. 5:6, 7) Kaya tikuphunzira mutu wanji, tizionetsetsa kuti tikuthandiza wophunzirayo kudziwa bwino makhalidwe a Yehova. Muzimuthandiza kudziwa kuti Yehova ali ndi makhalidwe abwino monga chikondi, kukoma mtima komanso chifundo. Yesu ananena kuti “lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba” ndi loti “uzikonda Yehova Mulungu wako.” (Mat. 22:37, 38) Choncho muziyesetsa kuthandiza wophunzira wanu kuti azikonda kwambiri Yehova. w20.10 10 ¶12

Lolemba, August 15

Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.​—Yoh. 11:5.

Yesu ankalemekeza akazi onse. (Yoh. 4:27) Koma ankalemekeza kwambiri akazi amene ankachita chifuniro cha Atate wake. N’zochititsa chidwi kuti Yesu ankaona akazi ngati alongo ake. Ndipo ananena kuti akaziwo komanso amuna ena anali mbali ya banja lake lauzimu. (Mat. 12:50) Yesu ankapezanso nthawi yocheza ndi alongo ndipo anali mnzawo weniweni. Iye ankacheza ndi Mariya komanso Malita, omwe anali alongo osakwatiwa. (Luka 10:38-42) Zimene ankalankhula komanso kuchita zinkapangitsa alongowa kuti azimasuka naye. Mwachitsanzo, Mariya anamasuka kukhala pamapazi a Yesu monga wophunzira wake. Komanso Malita, yemwe anakhumudwa chifukwa chakuti Mariya sankamuthandiza ntchito, anali womasuka kuuza Yesu zimene zinali m’maganizo mwake. Pa nthawiyi, Yesu anaphunzitsa alongo awiriwa mfundo zofunika. Anasonyezanso kuti ankawaganizira alongowa komanso mchimwene wawo Lazaro, chifukwa ankawayendera nthawi zina. (Yoh. 12:1-3.) N’zosadabwitsa kuti Lazaro atadwala kwambiri Mariya ndi Malita ankadziwa kuti akhoza kupempha thandizo kwa Yesu.​—Yoh. 11:3. w20.09 20 ¶3; 21 ¶6

Lachiwiri, August 16

Anthu anali kuganiza kuti ufumu wa Mulungu uonekera nthawi yomweyo.​—Luka 19:11.

JOphunzira a Yesu ankafunitsitsa Ufumu wa Mulungu utabwera “nthawi yomweyo,” kuti udzawapulumutse ku ulamuliro wankhanza wa Aroma. Nafenso timayembekezera mwachidwi nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzachotse zoipa zonse, n’kubweretsa dziko lomwe mudzakhale anthu omvera Mulungu. (2 Pet. 3:13) Komabe tikufunika kuyembekezera moleza mtima kufikira pamene Yehova adzachite zimenezi. Yehova anapereka nthawi yokwanira kwa Nowa kuti amange chingalawa komanso kuti agwire ntchito yake monga “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5; 1 Pet. 3:20) Komanso Yehova ankamvetsera mwatcheru pamene Abulahamu anamufunsa mobwerezabwereza, zokhudza cholinga chake chofuna kuwononga anthu oipa a mumzinda wa Sodomu ndi Gomora. (Gen. 18:20-33) Kwa zaka zambiri, Yehova anachitanso zinthu moleza mtima ndi mtundu wosakhulupirika wa Aisiraeli. (Neh. 9:30, 31) Masiku anonso Yehova amasonyeza kuti amalezera mtima anthu onse amene amafuna kukhala naye pa ubwenzi, powapatsa nthawi yokwanira yoti “alape.” (2 Pet. 3:9; Yoh. 6:44; 1 Tim. 2:3, 4) Chitsanzo cha Yehova chimatithandiza kuti nafenso tipitirizebe kulalikira komanso kuphunzitsa anthu moleza mtima. w20.09 10 ¶8-9

Lachitatu, August 17

Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.​—Mac. 24:15.

Yehova akamadzaukitsa anthu adzabwezeretsa zonse zokhudza anthuwo, monga zimene ankadziwa komanso makhalidwe awo. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amatikonda kwambiri moti amadziwa komanso amakumbukira zimene timaganiza, kulankhula, kuchita ndiponso mmene timamvera. Choncho sangavutike kutiukitsa monga mmene tinalili tisanamwalire. Nayenso Mfumu Davide ankadziwa kuti Yehova amadziwa bwino munthu aliyense payekha. (Sal. 139:1-4) Kodi timamva bwanji tikaganizira kuti Yehova amatidziwa bwino kwambiri? Kuganizira mfundo yoti Yehova amatidziwa bwino, kungatithandize kuti tisamadere nkhawa. N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani kuti Yehova amatikonda kwambiri. Iye amaona kuti munthu aliyense payekha ndi wamtengo wapatali ndipo amachita chidwi ndi zinthu zimene zimatichitikira. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri. Choncho sitiyenera kumadzimva kuti tili tokhatokha. Nthawi zonse Yehova amakhala nafe pafupi ndipo ndi wofunitsitsa kutithandiza.​—2 Mbiri 16:9. w20.08 17 ¶13-14

Lachinayi, August 18

Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.​—Sal. 32:8.

Yehova amakonda kuphunzitsa anthu ake. Iye amafuna kuti anthuwo amudziwe, kumukonda komanso kuti adzakhale ndi moyo wosatha monga ana ake okondedwa. Zimenezi sizingatheke ngati Yehova sangaphunzitse anthu akewo. (Yoh. 17:3) Yehova anagwiritsa ntchito mpingo wa Akhristu oyambirira pophunzitsa anthu ake. (Akol. 1:9, 10) Mzimu woyera womwe ndi “mthandizi” amene Yesu analonjeza, unathandiza kwambiri ophunzira. (Yoh. 14:16) Unawathandiza kuti azimvetsa bwino kwambiri Mawu a Mulungu. Unawathandizanso kuti azikumbukira zonse zimene Yesu ananena komanso kuchita zimene kenako zinalembedwa m’Mauthenga abwino. Zimene ankaphunzirazo zinathandiza Akhristuwo kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba, azikonda Mulungu ndi Mwana wake komanso kuti azikondana. Yehova ananeneratu kuti “m’masiku otsiriza,” anthu amitundu yonse adzakhamukira kuphiri lake lophiphiritsira kuti akawaphunzitse njira zake. (Yes. 2:2, 3) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa masiku ano. w20.10 24 ¶14-15

Lachisanu, August 19

Munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake.​—Miy. 1:5.

Kodi n’chiyani chingachititse munthu kukana malangizo abwino amene mnzake wamupatsa? Chimene chingachititse ndi kunyada. Anthu onyada amakonda kumva zinthu “zowakomera m’khutu.” Iwo safuna “kumvetsera choonadi.” (2 Tim. 4:3, 4) Anthuwa amaganiza kuti sakufunikira malangizo chifukwa amadziona kuti ndi anzeru komanso ofunika kuposa ena. Koma mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero, akudzinyenga.” (Agal. 6:3) Mfumu Solomo anafotokozanso bwino mfundo imeneyi. Iye analemba kuti: “Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino kuposa mfumu yokalamba koma yopusa, imene sionanso kufunika kochenjezedwa.” (Mlal. 4:13) Taganizirani zimene mtumwi Petulo anachita mtumwi Paulo atamudzudzula pamaso pa anthu ena. (Agal. 2:11-14) Petulo akanatha kumukwiyira Paulo chifukwa cha mmene anamulankhulira komanso chifukwa choti panali pagulu. Koma Petulo anachita zinthu mwanzeru ndipo anamvera malangizowo komanso sanamusungire Paulo chakukhosi. M’malomwake, patapita nthawi anamutchula Paulo kuti “m’bale wathu wokondedwa.”​—2 Pet. 3:15. w20.11 21 ¶9, 11-12

Loweruka, August 20

Mukaphunzitse anthu . . .  kuti akhale ophunzira anga. . . .  ndi kuwaphunzitsa.​—Mat. 28:19,20.

Kodi n’chiyani chingathandize kwambiri ophunzira Baibulo kuti akhale ophunzira a Yesu? Ndi kupezeka pamisonkhano yathu. Malangizo a m’Malemba amene angalandire pamisonkhanoyi angawathandize kuti adziwe zinthu zambiri, alimbitse chikhulupiriro chawo ndiponso kuti azikonda kwambiri Mulungu. (Mac. 15:30-32) Komanso wofalitsa angauze wophunzira Baibulo mmene kukonda kwambiri Yehova kunamuthandizira kuti azimvera malamulo ake. (2 Akor. 7:1; Afil. 4:13) Ndiyeno ophunzira Baibulo akadziwana ndi ofalitsa okhulupirika osiyanasiyana, angatengere chitsanzo chawo pa nkhani yomvera lamulo la Khristu lakuti tizikonda Mulungu ndi anthu ena. (Yoh. 13:35; 1 Tim. 4:12) Ndiponso akamaona ofalitsa amene akulimbana ndi mavuto ofanana ndi amene iwonso akulimbana nawo, zingawathandize kuona kuti n’zotheka kuti nawonso asinthe n’kukhala ophunzira a Khristu. (Deut. 30:11) Aliyense mumpingo angathandize m’njira zosiyanasiyana kuti ophunzira Baibulo afike pokhala ophunzira a Khristu.​—Mat. 5:16. w20.11 5 ¶10-12

Lamlungu, August 21

Ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso.​—1 Akor. 15:32.

N’kutheka kuti mtumwi Paulo ankanena zomenyana ndi zilombo zenizeni m’bwalo la masewera ku Efeso. (2 Akor. 1:8; 4:10; 11:23) Kapenanso ankanena za Ayuda ndi anthu ena ankhanza amene anali ngati “zilombo zakutchire.” (Mac. 19:26-34; 1 Akor. 16:9) Kaya ankanena za chiyani, Paulo anakumana ndi mavuto aakulu komabe ankakhulupirira kuti m’tsogolo adzakhala ndi moyo wosangalala. (1 Akor. 15:30, 31; 2 Akor. 4:16-18) Tikukhala mu nthawi yoopsa. Abale athu ena achitiridwa zinthu zankhanza. Ena akukhala m’madera omwe mukuchitika nkhondo ndipo amaona kuti ndi osatetezeka. Pamene m’mayiko ena anthu a Yehova alibe ufulu wolalikira koma amamutumikirabe ngakhale kuti akudziwa kuti akhoza kumangidwa kapena kuphedwa. Abale ndi alongo onsewa akupitirizabe kulambira Yehova ndipo ndi zitsanzo zabwino kwambiri kwa ife. Iwo sachita mantha chifukwa akudziwa kuti ngakhale atafa panopa, Yehova akulonjeza kuti adzawapatsa zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo. w20.12 9 ¶3-4

Lolemba, August 22

Ndife antchito anzake a Mulungu. Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa, nyumba ya Mulungu.​—1 Akor. 3:9.

Kodi munayamba mwafookapo chifukwa chakuti anthu a m’gawo lanu sachita chidwi ndi uthenga wanu, kapena chifukwa choti simuwapeza panyumba mukamalalikira? Zikatere, kodi tingatani kuti tipitirizebe kukhala osangalala? M’pofunika kuti tiziona moyenera ntchito yolalikira. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Tizikumbukira kuti timalalikira n’cholinga chothandiza anthu kudziwa dzina la Mulungu komanso kuwauza za Ufumu wake. Yesu ananena momveka bwino kuti ndi anthu ochepa omwe adzamutsatire. (Mat. 7:13, 14) Tikakhala mu utumiki timakhala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Yehova, Yesu komanso angelo. (Mat. 28:19, 20; Chiv. 14:6, 7) Yehova amakoka anthu omwe akufuna kumutumikira. (Yoh. 6:44) Choncho ngati munthu sanamvetsere uthenga wathu pa nthawiyi tingayembekezere kuti adzamvetsera nthawi ina. Mlongo wina dzina lake Deborah anati: “Satana amayesetsa kutifooketsa n’cholinga choti atigonjetse.” Koma Yehova Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana. w20.12 26 ¶18-19; 27 ¶21

Lachiwiri, August 23

Tiyeni tipitirize kukondana, chifukwa chikondi chimachokera kwa Mulungu.​—1 Yoh. 4:7.

Akhristu ambiri okhulupirika amayenera kugwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wawo komanso azisamalira mabanja awo. Komabe, iwo amachita zonse zimene angathe pothandiza gulu la Mulungu. Mwachitsanzo, ena amagwira nawo ntchito yothandiza pakachitika ngozi, ena pa ntchito zomangamanga ndipo aliyense ali ndi mwayi wopereka ndalama zothandiza pa Ntchito Yapadziko Lonse. Akhristuwa amachita zimenezi chifukwa amakonda Mulungu komanso anthu ena. Mlungu uliwonse, timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu tikamayesetsa kupezeka komanso kuyankha pamisonkhano. Ndipotu timayankha ngakhale pamene tili ndi mantha. Timayesetsanso kuchita zimenezi ngakhale kuti nthawi zina timakhala titatopa. Ngakhale kuti tonsefe tili ndi mavuto athu, timalimbikitsa ena misonkhano isanayambe komanso pambuyo pamisonkhano. (Aheb. 10:24, 25) Timayamikira kwambiri zimene abale ndi alongo athu okondedwawa amachita. w21.01 10 ¶11

Lachitatu, August 24

Tisakhale odzikuza.—Agal. 5:26.

Anthu onyada zimawavuta kuti ayamikire ena chifukwa amaona kuti iwowo ndi amene ayenera kutamandidwa. Nthawi zambiri iwo amakonda kudziyerekezera ndi ena komanso amalimbikitsa mzimu wampikisano. M’malo mophunzitsa ena kuti azichita zinazake kapena kuwapatsa udindo, anthu onyada amaganiza kuti ayenera kuchita chilichonse okha chifukwa amaona kuti ena sangakwanitse kuchita bwino ngati mmene iwowo amachitira. Nthawi zambiri, munthu wonyada amafuna azioneka kuti ndi wofunika kuposa ena, ndiye ena akamachita bwino kuposa iyeyo amawachitira nsanje. Ngati tazindikira kuti tayamba kunyada, tiyenera kupempha mochokera pansi pa mtima kuti Yehova atithandize ‘kusintha maganizo athu,’ kuti mtima wonyadawu usatilowerere. (Aroma 12:2) Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatisonyeza mmene tingakhalire odzichepetsa. (Sal. 18:35) Timaona kuti iye ndi wodzichepetsa tikaona mmene amachitira zinthu ndi atumiki ake ndipo timafuna kumutsanzira. Komanso tikufuna kutsanzira zitsanzo zabwino za anthu otchulidwa m’Baibulo omwe anayenda modzichepetsa ndi Mulungu. Nthawi zonse tiziyesetsa kulemekeza Yehova komanso kumupatsa ulemelero womwe amayenera kulandira.​—Chiv. 4:11. w20.08 13 ¶19-20

Lachinayi, August 25

Olowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.—1 Akor. 7:28.

Ukwati ndi mphatso yangwiro yochokera kwa Mulungu, koma anthufe si angwiro. (1 Yoh. 1:8) N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amachenjeza anthu amene ali pabanja kuti adzakumana ndi mavuto, omwe amafotokozedwa kuti ndi “nsautso m’thupi mwawo.” Yehova amayembekezera amuna a Chikhristu kuti azipezera anthu a m’banja lawo zinthu zofunika pa moyo, kuwathandiza kuti aziona kuti ndi otetezeka komanso kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi iye. (1 Tim. 5:8) Komabe alongo amene ali pabanja, tsiku lililonse amayenera kupeza nthawi yowerenga mawu a Mulungu, kuganizira mozama zimene awerengazo komanso kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Akazi amatanganidwa kwambiri, choncho akhoza kumaona ngati alibe nthawi komanso mphamvu yochitira zonsezi, komabe iwo ayenera kuona kuti kupeza nthawi yochita zimenezi n’kofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova amafuna kuti aliyense payekha apitirizebe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi iye. (Mac. 17:27) Kunena zoona, mkazi ayenera kuchita khama kuti azigonjera mwamuna wake yemwe si wangwiro. Komabe iye angakwanitse udindo umene Yehova anamupatsa akamvetsa komanso kuvomereza chifukwa chake Baibulo limanena kuti akazi ayenera kugonjera amuna awo. w21.02 9 ¶3, 6-7

Lachisanu, August 26

Chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.​—Yak. 1:3.

Mayesero tingawayerekezere ndi moto umene amagwiritsa ntchito popanga chitsulo kuti chikhale cholimba. Chitsulocho chimaikidwa pamoto ndipo chikazizira chimakhala cholimba kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, tikapirira mayesero chikhulupiriro chathu chimalimba. N’chifukwa chake Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse.” (Yak. 1:4) Tikamaona kuti mayesero akutithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, tingathe kuwapirira mosangalala. M’kalata yake, Yakobo anatchulanso zinthu zina zimene zingachititse kuti tisamasangalale. Vuto lina limene limakhalapo ndi kulephera kudziwa zoyenera kuchita. Tikakumana ndi mayesero timafuna kuti Yehova atithandize kuti tisankhe zimene iye angasangalale nazo, zimene zingathandize abale ndi alongo athu komanso zimene zingatithandize kupitirizabe kukhala okhulupirika. (Yer. 10:23) Timafunika nzeru kuti tidziwe zoyenera kuchita komanso kulankhula, anthu ena akamatitsutsa. Ngati sitikudziwa zoyenera kuchita tikakumana ndi mavuto enaake, tikhoza kutaya mtima ndipo zimenezi zingachititse kuti tisamasangalale. w21.02 28 ¶7-9

Loweruka, August 27

Kondanani kwambiri kuchokera mumtima.​—1 Pet. 1:22.

Yehova amatipatsa chitsanzo pankhaniyi. Iye amatikonda kwambiri, moti ngati titapitirizabe kukhala okhulupirika palibe chimene chingachititse kuti asiye kutikonda. (Aroma 8:38, 39) Mawu akuti ‘kukondana kwambiri’ akutichititsa kuganiza za munthu amene akuyesetsa kuchita zinthu zosonyeza kuti amakonda ena. Nthawi zina zingamativute kusonyeza chikondi kwa abale ndi alongo athu. Ena akatikhumudwitsa tiyenera kupitirizabe ‘kulolerana m’chikondi, tiziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere, umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.’ (Aef. 4:1-3) Tisamaganizire kwambiri zimene abale ndi alongo athu amalakwitsa. M’malomwake tiziyesetsa kuti tiziwaona mmene Yehova amawaonera. (1 Sam. 16:7; Sal. 130:3) Nthawi zina zimakhala zovuta kusonyeza chikondi chenicheni kwa abale ndi alongo athu makamaka ngati tikudziwa zimene amalakwitsa. Ndipo limeneli ndi vuto limene Akhristu ena mu nthawi ya atumwi anali nalo, monga Eodiya ndi Suntuke. Choncho mtumwi Paulo anawalimbikitsa “kuti akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.”​—Afil. 4:2, 3. w21.01 22-23 ¶10-11

Lamlungu, August 28

Ndikulembera inu anyamata chifukwa ndinu olimba ndipo mawu a Mulungu akhaladi mwa inu ndiponso mwagonjetsa woipayo.​—1 Yoh. 2:14.

Achikulire amasangalala achinyamatanu mukamatumikira nawo limodzi Yehova “mogwirizana.” (Zef. 3:9) Iwo amayamikira kwambiri khama lanu komanso kudzipereka kwanu pogwira ntchito iliyonse imene mwapatsidwa. Ndipotu iwo amakukondani kwambiri. Achinyamatanu, muzikumbukira kuti Yehova amakukondani ndipo amakudalirani. Iye ananeneratu kuti m’masiku otsiriza padzakhala achinyamata ambiri amene azadzipereke mofunitsitsa kuti amutumikire. (Sal. 110:1-3) Yehova akudziwa kuti mumamukonda ndipo mumayesetsa kuchita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Choncho muzichita zinthu moleza mtima mukamachita zinthu ndi anthu ena komanso panokha. Mukalakwitsa zinazake, muzivomereza ena akakupatsani uphungu kapena malangizo ndipo muziona kuti akuchokera kwa Yehova. (Aheb. 12:6) Muzichita khama kugwira ntchito iliyonse imene mwapatsidwa. Ndipo koposa zonse, pa chilichonse chimene mukuchita, muziyesetsa kusangalatsa Atate wanu wakumwamba.​—Miy. 27:11. w21.03 7 ¶17-18

Lolemba, August 29

Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.—Miy. 24:10.

Tingathe kufooka chifukwa cha mavuto osiyanasiyana. Mavuto ena angakhale oyambitsidwa ndi ifeyo, ndipo ena angayambe chifukwa cha zinthu zina. Zinthu zimenezi zingakhale zimene timalakwitsa, zimene sitingakwanitse kuchita kapena matenda. Tingathenso kufooka chifukwa sitinapatsidwe utumiki umene timalakalaka m’gulu la Yehova, kapena chifukwa chakuti tikulalikira m’gawo limene anthu ambiri samvetsera uthenga wathu. N’zosavuta kumadziona ngati wopanda pake komanso kumadziimba mlandu chifukwa cha zinthu zimene talakwitsa. Zimenezi zingapangitse kuti tiziganiza kuti chifukwa cha zimene timalakwitsa Yehova sangafune kuti tikalowe m’dziko latsopano. Maganizo amenewa ndi oopsa kwambiri. Baibulo limanena kuti kupatulapo Yesu Khristu yekha, anthu onse ndi “ochimwa.” (Aroma 3:23) Koma Yehova samangoyang’ana zimene timalakwitsa kapena kuyembekezera kuti tizichita zinthu mosalakwitsa chilichonse. M’malomwake Iye ndi atate wachikondi amene amafuna kutithandiza. Komanso ndi woleza mtima. Ndipo akudziwa kuti ambirife tikuyesetsa kuti tizichita zinthu zabwino komanso kuti tisamadzione ngati opanda pake ndipo Iye ndi wokonzeka kutithandiza.​—Aroma 7:18, 19. w20.12 22 ¶1-3

Lachiwiri, August 30

Pomalizira abale, ndikuti pitirizani kukondwera, kusintha maganizo anu.​—2 Akor. 13:11.

Tonsefe tili pa ulendo. Ulendo wake ndi wopita m’dziko latsopano lolamulidwa ndi Yehova, yemwe ndi wolamulira wachikondi. Tsiku lililonse timayesetsa kuyenda panjira imene ingatitsogolere ku moyo. Koma monga mmene Yesu ananenera, njira ya ku moyoyi ndi yopanikiza ndipo nthawi zina imakhala yovuta kuyendamo. (Mat. 7:13, 14) Popeza si ife angwiro, n’zosavuta kuchoka panjirayi.(Agal. 6:1) Kuti tipitirize kuyenda panjira yopanikiza ya ku moyo, tiyenera kukhala ofunitsitsa kusintha mmene timaganizira komanso zochita zathu. Mtumwi Paulo akutilimbikitsa “kusintha maganizo” athu. Nthawi zambiri zimativuta kufufuza maganizo athu komanso mmene timamvera. Izi zili choncho chifukwa choti mtima wathu ndi wonyenga ndipo zimenezi zingachititse kuti kukhale kovuta kudziwa zomwe mtimawu ungatilimbikitse kuchita. (Yer. 17:9) N’zosavuta kuti tizidzipusitsa ndi “maganizo onama.” (Yak. 1:22) Choncho, tikamadzifufuza tiyenera kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Mawu a Mulunguwa amatithandiza kudziwa mmene tilili chifukwa amatha kuzindikira “zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.”​—Aheb. 4:12, 13. w20.11 18 ¶1-3

Lachitatu, August 31

Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.​—Aroma 12:10.

Kukhala odzichepetsa kumatithandiza kuti tizisangalala. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikamadziwa kuti pali zina zimene sitingakwanitse kuchita, timayamikira anthu ena akatithandiza. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Yesu atachiritsa anthu 10 akhate. Mmodzi yekha ndi amene anabwerera kukamuthokoza chifukwa chomuchiritsa matenda ake oopsawo. Munthuyu anali wodzichepetsa ndipo ankadziwa kuti sakanatha kuchira popanda kuthandizidwa ndi Yesu. Iye anayamikira thandizo lomwe anapatsidwa ndipo analemekeza Mulungu. (Luka 17:11-19) Anthu odzichepetsa amagwirizana ndi ena ndipo savutika kupeza anzawo abwino. Izi zili choncho chifukwa amazindikira kuti anthu ena ali ndi makhalidwe abwino ndipo zimakhala zosavuta kuti awakhulupirire. Anthu odzichepetsa amasangalala anthu ena zikamawayendera bwino ndipo anthuwo akachita zinthu zabwino amawayamikira komanso kuwalemekeza. w20.08 12 ¶17-18

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena