Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es22 tsamba 88-98
  • September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
  • Timitu
  • Lachinayi, September 1
  • Lachisanu, September 2
  • Loweruka, September 3
  • Lamlungu, September 4
  • Lolemba, September 5
  • Lachiwiri, September 6
  • Lachitatu, September 7
  • Lachinayi, September 8
  • Lachisanu, September 9
  • Loweruka, September 10
  • Lamlungu, September 11
  • Lolemba, September 12
  • Lachiwiri, September 13
  • Lachitatu, September 14
  • Lachinayi, September 15
  • Lachisanu, September 16
  • Loweruka, September 17
  • Lamlungu, September 18
  • Lolemba, September 19
  • Lachiwiri, September 20
  • Lachitatu, September 21
  • Lachinayi, September 22
  • Lachisanu, September 23
  • Loweruka, September 24
  • Lamlungu, September 25
  • Lolemba, September 26
  • Lachiwiri, September 27
  • Lachitatu, September 28
  • Lachinayi, September 29
  • Lachisanu, September 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
es22 tsamba 88-98

September

Lachinayi, September 1

Zimenezi zikadzachitika ndidzatsanulira mzimu wanga pa chamoyo chilichonse.​—Yow. 2:28.

Mulungu anauzira Petulo kuti asinthe pang’ono mawu a mu ulosi wa Yoweli. (Mac. 2:16, 17) M’malo moyamba ndi mawu akuti “zimenezi zikadzachitika,” anayamba ndi mawu akuti: “Ndipo m’masiku otsiriza” Mulungu adzatsanulira mzimu wake “pa anthu osiyanasiyana.” Ponena kuti “m’masiku otsiriza,” ankatanthauza kuti Yerusalemu ndi kachisi wake atatsala pang’ono kuwonongedwa. Izi zikusonyeza kuti panapita nthawi yaitali ulosi wa Yoweli usanakwaniritsidwe. Mzimu woyera utaperekedwa mu 33 C.E. m’pamene ntchito yolalikira inayamba kufalikira kwambiri. Pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Akhristu a ku Kolose cha m’ma 61 C.E., ananena kuti uthenga wabwino “unali utalalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Mawu oti “m’chilengedwe chonse” palembali akutanthauza madera onse amene ankadziwika pa nthawiyo. Mzimu wa Yehova wathandizanso kuti pofika pano uthenga wabwino ukhale utalalikidwa “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Mac. 13:47. w20.04 6-7 ¶15-16

Lachisanu, September 2

Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.​—Ezek. 34:11.

Yehova amatikonda tonsefe kuphatikizapo anthu amene asiya kumutumikira. (Mat. 18:12-14) Mulungu analonjeza kuti adzafunafuna nkhosa zake zosochera n’kuzithandiza kuti zikhalenso naye pa ubwenzi wabwino. Ndipo iye anafotokoza zimene adzachite pofuna kupulumutsa atumiki akewo. Zimene anafotokozazo ndi zomwenso m’busa wachiisiraeli ankachita ngati nkhosa yake yasowa. (Ezek. 34:12-16) Choyamba, m’busa ankasakasaka nkhosayo, zimene zinkafunika nthawi yambiri komanso khama. Ndiye akaipeza, amaibweretsa kugulu la nkhosa zake. Kuwonjezera apo, ngati nkhosayo yavulala kapena ili ndi njala, m’busayo ankaithandiza pomanga mabala ake, kuinyamula komanso kuidyetsa. Akulu, omwe ndi abusa a “gulu la nkhosa za Mulungu” ayeneranso kuchita zofanana ndi zimenezi akamathandiza anthu amene asiya kusonkhana. (1 Pet. 5:2, 3) Akulu amafufuza anthu amenewa, kuwathandiza kuti abwerere mumpingo komanso kuwasonyeza chikondi powathandiza kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. w20.06 20 ¶10

Loweruka, September 3

M’mindamo mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.—Yoh. 4:35.

Kodi Yesu anaona kuti minda inali yofunika kukolola chifukwa chakuti ankayembekezera kuti anthu ambiri adzamutsatira? Ayi. Malemba anali ataneneratu kuti anthu ochepa ndi amene adzamukhulupirira. (Yoh. 12:37, 38) Ndipo Yesu anali ndi luso lodziwa zamumtima wa munthu. (Mat. 9:4) Ngakhale zinali choncho, ankalalikira kwa anthu onse koma ankathandiza kwambiri anthu ochepa omwe akanatha kumukhulupirira. Choncho popeza ifeyo sitingadziwe zamumtima wa munthu, tiyenera kupewa kuweruza anthu. M’malomwake, tiyenera kuona kuti munthu aliyense akhoza kukhala wophunzira. Kumbukirani zimene Yesu anauza ophunzira ake. Iye ananena kuti m’minda ndi moyera, kapena kuti ndi mofunika kukolola. Anthu amatha kusintha n’kukhala ophunzira a Khristu. Yehova amaona kuti anthuwo ali ngati “zinthu zamtengo wapatali.” (Hag. 2:7) Ngati timaona anthu mmene Yehova ndi Yesu amawaonera, tidzayesetsa kudziwa za moyo wawo komanso zimene amakonda. Sitidzawaona ngati anthu achilendo koma ngati anthu amene akhoza kudzakhala abale ndi alongo athu. w20.04 13 ¶18-19

Lamlungu, September 4

Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.​—Yoh. 15:15.

Mawu a Mulungu amaphunzitsa momveka bwino kuti tiyenera kukonda Yesu kuti tizisangalatsa Yehova. Chinthu chimodzi chimene tingachite kuti tikhale anzake a Yesu ndi choti tiyenera kumudziwa bwino. Tingaphunzire za moyo wa Yesu powerenga mabuku a m’Baibulo a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Tikamaganizira nkhani za m’mabukuwa timaona kuti Yesu ankachitira chifundo anthu ndipo izi zimachititsa kuti tizimukonda komanso kumulemekeza. Mwachitsanzo, ngakhale kuti iye anali Ambuye wa ophunzira ake, sankachita nawo zinthu ngati akapolo ake. Koma ankawafotokozera maganizo ake ndi zimene zinali mumtima mwake. Yesu akaona otsatira ake akuvutika zinkamupweteka kwambiri ndipo ankalira nawo. (Yoh. 11:32-36) Ngakhale anthu amene ankadana naye anavomereza kuti iye ankagwirizana ndi anthu amene ankamvetsera uthenga wake. (Mat. 11:19) Tikamatsanzira zimene Yesu ankachitira ophunzira ake, timayamba kugwirizana ndi anzathu, timakhala osangalala komanso timayamba kukonda kwambiri Khristu. w20.04 22 ¶9-10

Lolemba, September 5

Mfumu ya kum’mwera nayonso idzakonzekera nkhondo mwa kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.​—Dan. 11:25.

Pofika mu 1870, dziko la Britain linkalamulira mayiko ambiri kuposa mayiko ena onse ndipo linkaposa mayiko onse pankhondo. Ulamulirowu ndi womwe unatchulidwa ngati nyanga yaing’ono yomwe inagonjetsa nyanga zina zitatu, zomwe ndi mayiko a France, Spain ndi Netherlands. (Dan. 7:7, 8) Choncho ulamuliro wa Britain ndi umene unali mfumu ya kum’mwera mpaka pa nthawi yankhondo yoyamba ya padziko lonse. Pa nthawiyi dziko la United States of America linali lolemera kwambiri padziko lonse ndipo linayamba kuchita mgwirizano ndi dziko la Britain. Pa nthawi yankhondo yoyamba ya padziko lonse mayiko a United States ndi Britain ankamenyera limodzi nkhondo. Mgwirizano umene anapangawu, unachititsa kuti akhale amphamvu kwambiri padziko lonse. Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, mfumuyi inasonkhanitsa “gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.” Mu nthawi yonse yamapeto, mayiko a Britain ndi America ndi amene akhala mfumu ya kum’mwera. w20.05 4 ¶7-8

Lachiwiri, September 6

Mitsinjeyo imabwerera kumalo kumene inachokera.​—Mlal. 1:7.

Dzikoli linatalikirana ndi dzuwa pamtunda wabwino moti madzi satentha kwambiri n’kukhala nthunzi kapena kuzizira kwambiri mpaka kuundana. Koma ngati likanayandikira pang’ono, madzi onse akanauma ndipo padzikoli pakanakhala potentha kwambiri komanso popanda zamoyo. Ndipo ngati likanatalikiranso pang’ono, madzi onse akanaundana ndipo dziko lonseli likanakhala ayezi yekhayekha. Choncho Yehova anaika dziko ndi dzuwa pamtunda wabwino zimene zimachititsa kuti padzikoli pakhale madzi omwe amathandiza zamoyo. Dzuwa likawala, madzi apadzikoli amakwera m’mwamba ngati nthunzi ndipo imakakhala mitambo. Chaka chilichonse, madzi amene amakwera m’mwambawa akhoza kudzaza madamu 500,000. Damu lililonse kukula kwake kilomita imodzi m’litali, m’lifupi komanso kuya kwake. Madziwa amakhala m’mlengalenga kwa masiku pafupifupi 10 asanagwe ngati mvula kapena sinowo. Zikatero madziwo amabwereranso m’nyanja kapena m’mitsinje ndipo zimenezi zimachitika mobwerezabwereza. Izi zimasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wanzeru komanso wamphamvu.​—Yobu 36:27, 28. w20.05 22 ¶6

Lachitatu, September 7

Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.​—Mac. 1:8.

Yesu anatilimbikitsa kuti tizipempha mzimu woyera. (Luka 11:9, 13) Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Yehova amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Mzimu wa Mulungu ungatithandize kuti tithe kupirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo. Mzimu woyera umatithandizanso kuti tikwanitse kuchita mautumiki osiyanasiyana ndipo ungatithandize kukulitsa luso limene tingakhale nalo. Choncho timadziwa kuti zilizonse zimene timakwanitsa kuchita potumikira Mulungu zimatheka chifukwa iye amatithandiza ndi mzimu wake. Njira ina imene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso ya mzimu woyera ndi kupempha kuti uzitithandiza kudzifufuza kuti tione ngati tayamba kukhala ndi maganizo olakwika mumtima wathu. (Sal. 139:23, 24) Tikatero, Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake kutithandiza kuzindikira maganizo olakwikawo komanso zomwe tingachite kuti tiwapewe. Tikamachita zimenezi tingasonyeze kuti sitikufuna kuchita chilichonse chomwe chingachititse kuti Yehova asiye kutithandiza ndi mzimu wake woyera.​—Aef. 4:30. w20.05 28-29 ¶10-12

Lachinayi, September 8

Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.​—Yoh. 17:26.

Tikamateteza dzina la Mulungu timakhala tikutsanzira Yesu Khristu. Yesu anathandiza anthu kudziwa dzina la Atate wake. Sikuti iye ankangogwiritsa ntchito dzinali koma anathandizanso anthu kuti amudziwe bwino Mulungu. Mwachitsanzo, anatsutsa zonena za Afarisi zomwe zinkapangitsa anthu ena kuona kuti Yehova ndi wankhanza, wopanda chifundo komanso saganizira anthu. Yesu anathandiza anthu kudziwa kuti Atate wake amachita zinthu moganizira ena, ndi wachifundo, wachikondi komanso wokhululuka. Anathandizanso anthu kudziwa bwino mmene Yehova alili chifukwa tsiku lililonse ankasonyeza makhalidwe amene anatengera kwa Atate wake. (Yoh. 14:9) Mofanana ndi Yesu, nafenso tingauze anthu ena zimene tikudziwa zokhudza Yehova komanso kuwaphunzitsa kuti iyeyo ndi Mulungu wachikondi ndiponso wokoma mtima. Tikamachita zimenezi, timakhala tikusonyeza kuti zoipa zimene otsutsa amamunenera ndi zabodza. Timayeretsa dzina la Mulungu tikamathandiza anthu kuti aziliona kuti ndi loyera. Tikamalankhula komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi makhalidwe a Yehova, timathandiza kuyeretsa dzina lake. Timayeretsanso dzinali tikamaphunzitsa anthu kuti adziwe zoona zokhudza Mulungu. w20.06 6 ¶17-18

Lachisanu, September 9

Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.​—Agal. 5:26.

N’zoona kuti intaneti ndi yothandiza. Mwachitsanzo, tingaigwiritse ntchito polankhulana ndi achibale komanso anzathu. Koma kodi mumaona kuti zinthu zina zomwe anthu amaika pa intaneti zimangokhala zofuna kuti anthu ena aziwasirira? Zikuoneka kuti iwo amangofuna kuti anthu ena azichita nawo chidwi. Ena amalemba mawu achipongwe kapena otukwana pa zithunzi zimene iwowo kapena anthu ena aika pa intaneti. Kuchita zimenezi si kudzichepetsa komanso si kumvera ena chisoni omwe ndi makhalidwe amene Akhristu amalimbikitsidwa kukhala nawo. (1 Pet. 3:8) Ngati mumagwiritsa ntchito intaneti, dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene ndimalemba pa intaneti komanso zithunzi kapena mavidiyo amene ndimaikapo, zimapangitsa ena kuona kuti ndine wonyada? Kodi zingapangitse ena kuyamba kuchita nsanje?’ Komatu Akhristu sayenera kumadziona kuti ndi ofunika kwambiri kapenanso kukhala ndi maganizo oti anthu ena aziwasirira. Iwo amatsatira malangizo a m’lemba laleroli. Kudzichepetsa kungatithandize kupewa makhalidwe a anthu am’dzikoli omwe ndi onyada ndipo amafuna kuti ena aziwaona kuti ndi ofunika kwambiri.​—1 Yoh. 2:16. w20.07 6 ¶14-15

Loweruka, September 10

Kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe. Komabe anandichitira chifundo chifukwa ndinali wosadziwa.—1 Tim. 1:13.

Mtumwi Paulo asanakhale Mkhristu, anali munthu wachipongwe ndipo ankazunza otsatira a Yesu. (Mac. 7:58) Yesu analetsa Paulo, yemwe pa nthawiyo ankadziwika kuti Saulo, kuti asamazunze mpingo wa Chikhristu. Ali kumwamba, Yesu analankhula ndi Paulo ndipo anamuchititsa khungu. Kuti ayambirenso kuona, Paulo ankafunika kuthandizidwa ndi anthu omwe ankawazunza aja. Iye anadzichepetsa n’kulolera kuthandizidwa ndi Hananiya kuti ayambirenso kuona. (Mac. 9:3-9, 17, 18) Kenako Paulo anakhala munthu wodziwika bwino mumpingo wa Chikhristu. Koma sanaiwale zimene Yesu anamuphunzitsa panjira yopita ku Damasiko. Paulo anapitiriza kukhala wodzichepetsa ndipo ankalola kuti abale ndi alongo azimuthandiza. Iye ananena za Akhristu anzake ena kuti anamuthandiza komanso kumulimbikitsa.​—Akol. 4:10, 11. w20.07 18-19 ¶16-17

Lamlungu, September 11

Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.​—Luka 12:32.

Ngakhale kuti Yehova ndi Wamphamvuyonse, amapereka mphamvu kwa ena. Mwachitsanzo, iye anasankha Yesu kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake ndipo adzaperekanso mphamvu zina kwa anthu okwana 144,000 amene adzalamulire ndi Yesu. N’zosakayikitsa kuti Yehova anaphunzitsa Yesu kuti adzakhale Mfumu komanso mkulu wa ansembe. (Aheb. 5:8, 9) Amaphunzitsanso anthu amene adzalamulire ndi Yesu ndipo amawalola kuti akwaniritse maudindo awo popanda kulamulira zimene akuchita. M’malomwake, amawadalira kuti achita chifuniro chake. (Chiv. 5:10) Ngati Atate wathu wakumwamba yemwe safunikira kuthandizidwa ndi aliyense amapereka zochita kwa anthu ena, kuli bwanji ifeyo? Nafenso tiyenera kulola anthu ena kuti azichita zinthu zina. Mwachitsanzo, kodi ndinu mutu wa banja kapena ndinu mkulu mumpingo? Muzitsanzira Yehova popereka zochita kwa ena ndipo mukatero muzipewa kulamulira mmene akuchitira zinthuzo. Mukamatsanzira Yehova, ntchito zambiri zidzayenda bwino komanso mungaphunzitse ena ndi kuwathandiza kuti asamaope kugwira ntchito zina.​—Yes. 41:10. w20.08 9 ¶5-6

Lolemba, September 12

Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa anthu osochera.​—Luka 19:10.

Kodi Yehova amafuna kuti nkhosa zake zomwe zinasochera tiziziona bwanji? Tingaphunzire pa zomwe Yesu anachita. Yesu ankadziwa kuti nkhosa zonse za Yehova ndi zamtengo wapatali. Choncho ankachita zonse zomwe akanatha kuti athandize “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli” kuti zibwerere kwa Yehova. (Mat. 15:24) Komanso chifukwa chakuti Yesu anali m’busa wabwino, ankachita zonse zomwe akanatha kuti nkhosa iliyonse ya Yehova isatayike. (Yoh. 6:39) Mtumwi Paulo analimbikitsa akulu a mpingo wa ku Efeso kuti azitsanzira Yesu. Anawauza kuti: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.’” (Mac. 20:17, 35) Lembali likusonyeza kuti masiku anonso akulu ali ndi udindo wofunika kwambiri wosamalira nkhosa za Mulungu. Mkulu wina ku Spain ananena kuti: “Ndimaona kuti Yehova amadera nkhawa nkhosa zake zosochera ndipo zimenezi zimandilimbikitsa kuti inenso ndichite zonse zomwe ndingathe kuti ndithandize nkhosazi. Ndimadziwa kuti umenewu ndi udindo umene Yehova anandipatsa.” w20.06 23 ¶15-16

Lachiwiri, September 13

Zakalezo zapita.​—Chiv. 21:4.

Yehova adzapitiriza kuyembekezera moleza mtima kuti tikhale angwiro, mpaka kumapeto kwa zaka 1,000. Kufikira pa nthawiyo, Yehova akhala akutikhululukira machimo athu. Choncho nafenso tiyenera kumutsanzira poyesetsa kumaona makhalidwe abwino a anthu ena n’kumawalezera mtima. Yesu komanso angelo anasangalala dziko lapansi litangolengedwa. Koma taganizirani mmene adzasangalalire akadzaona dziko lonse litadzaza ndi anthu angwiro, omwe amakonda komanso kutumikira Yehova. Taganizirani mmene anthu omwe adzalamulire ndi Khristu adzamvere akadzaona anthu akupindula ndi ntchito yawo padzikoli. (Chiv. 4:4, 9-11; 5:9, 10) Tayerekezerani kuti muli m’dziko limene simudzakhalanso zopweteka zilizonse monga matenda, chisoni ndi imfa. Mpaka pa nthawi imeneyo, tiyeni titsimikize mtima kuti tizitsanzira Atate wathu wachikondi, wanzeru komanso woleza mtima. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti tizikhalabe osangalala ngakhale tikumane ndi mayesero. (Yak. 1:2-4) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha lonjezo lake lakuti “kudzakhala kuuka.”​—Mac. 24:15. w20.08 19 ¶18-19

Lachitatu, September 14

Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.​—Mat. 24:14.

Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Atate wathu wakumwamba anauzira anthu ena kuti alembe bukuli chifukwa choti amatikonda kwambiri. Yehova amagwiritsa ntchito Baibulo potiyankha mafunso ofunika kwambiri omwe timakhala nawo. Mafunso monga akuti: Kodi anthufe tinachokera kuti? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Kodi tiziyembekezera zotani m’tsogolomu? Yehova amafuna kuti tonse tidziwe mayankho a mafunso amenewa, choncho kuyambira kalekale wakhala akuthandiza anthu kuti amasulire Baibulo m’zilankhulo zambiri. Masiku ano, Baibulo lonse kapena mbali yake, limapezeka m’zilankhulo zoposa 3,000. Palibe buku lomwe linamasuliridwapo komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa Baibulo. Tingasonyeze kuyamikira Mulungu kuti anatipatsa Baibulo, tikamaliwerenga tsiku lililonse, kuganizira mozama zimene tikuphunzira komanso kuyesetsa kutsatira zimene tikuphunzirazo. Timasonyezanso kuyamikira tikamachita zonse zimene tingathe pouza ena uthenga wa m’Baibulo.​—Sal. 1:1-3; Mat. 28:19, 20. w20.05 24-25 ¶15-16

Lachinayi, September 15

Mawu a Yehova achititsa kuti ndizinyozedwa ndi kutonzedwa tsiku lonse.​—Yer. 20:8.

Gawo limene mneneri Yeremiya anauzidwa kuti azikalalikira linali lovuta kwambiri. Moti nthawi ina anafooka mpaka kufika pofuna kusiya kulalikira. Komabe sanasiye. N’chiyani chinamuthandiza? “Mawu a Yehova” anali ngati moto mumtima mwa Yeremiya, choncho sakanatha kungokhala osamalalikira. (Yer. 20:9) Zimenezinso ndi zomwe zingachitike kwa ife ngati timaphunzira Mawu a Mulungu tsiku lililonse komanso kuganizira mozama zimene timaphunzira. Tikamachita zimenezi, tingakhale osangalala ndi utumiki wathu komanso anthu ambiri angayambe kumvetsera uthenga wathu. (Yer. 15:16) Choncho mukaona kuti mwafooka muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Iye angatithandize kuti tisamadziimbe kwambiri mlandu chifukwa cha zinthu zimene timalakwitsa, zimene sitingakwanitse kuchita komanso angatithandize pamene tikudwala. Angatithandizenso kuti tiziona moyenera utumiki umene tikuchita ndiponso kuti tizisangalala tikamagwira ntchito yolalikira. Choncho muzipemphera kwa Atate wanu wakumwamba n’kumufotokozera mmene mukumvera. Iye adzakuthandizani kuti mupitirizebe kumutumikira ngakhale mukukumana ndi zinthu zimene zingakufooketseni. w20.12 27 ¶20-21

Lachisanu, September 16

Uwadandaulire . . . akazi achikulire ngati amayi ako, akazi achitsikana uwadandaulire ngati alongo ako, ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse oipa.​—1 Tim. 5:1, 2.

Kwa alongo ena, misonkhano imawapatsa mwayi wokhala ndi Akhristu anzawo. Choncho akabwera pamisonkhano tiyenera kuwalandira bwino, kulankhula nawo komanso kuwathandiza kudziwa kuti timawaganizira Mofanana ndi Yesu, nafenso tingachite bwino kumapeza nthawi yocheza ndi alongo. (Luka 10:38-42) Mwachitsanzo, tingawaitanire kunyumba kuti tidzadye nawo chakudya, kapena kuti tidzangocheza. Tikamachita zimenezi, tizionetsetsa kuti tikukambirana nkhani zolimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Akulu angachite bwino kukhala ndi maganizo ofanana ndi a Yesu. Yesu ankadziwa kuti n’zovuta kwa ena kumakhala okha. Koma iye anafotokoza momveka bwino kuti, kuti munthu akhale wosangalala sizimadalira kuti akhale pabanja kapena kuti akhale ndi ana. (Luka 11:27, 28) M’malo mwake tingapeze chimwemwe chenicheni ngati timaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri pa moyo wathu. (Mat. 19:12) Makamaka akulu ayenera kumaona akazi a Chikhristu monga alongo awo komanso amayi awo. Akulu ayenera kumapeza nthawi yocheza ndi alongo misonkhano isanayambe kapena ikatha. w20.09 21-22 ¶7-9

Loweruka, September 17

[Mlimi] amayembekezerabe zipatso zofunika kwambiri . . . Nanunso khalani oleza mtima.​—Yak. 5:7, 8.

Ku Isiraeli mlimi ankadzala mbewu zake mvula yoyambirira ikangogwa ndipo ankakolola mbewuzo zikakhwima chakumapeto kwa nyengo ya dzinja. (Maliko 4:28) Nafenso tingachite bwino kwambiri kukhala oleza mtima ngati mlimi. Komabe kuchita zimenezi sikophweka. Nthawi zambiri anthu ochimwafe, timafuna kuona zotsatira za ntchito yathu nthawi yomweyo. Koma ngati tikufuna tikolole mbewu m’munda wathu, tiyenera kumausamalira. Mwachitsanzo tiyenera kulima, kudzala, kupalira komanso kuthirira. Nayonso ntchito yophunzitsa anthu imafuna khama. Zimatenga nthawi kuti tithandize ophunzira Baibulo athu kusiya kukhala ndi mtima watsankho n’kuyamba kukonda ena. Kuleza mtima kungatithandizenso kuti tisafooke anthu ena akapanda kumvetsera uthenga wathu. Tingafunikebe kukhala oleza mtima, ngakhale titakumana ndi anthu omvetsera. Tikutero chifukwa sitingakakamize ophunzira Baibulo wathu kuti asinthe mofulumira kwambiri. Ngakhalenso ophunzira a Yesu nthawi zina ankavutika kumvetsa zimene Yesu ankawaphunzitsa. (Yoh. 14:9) Tizikumbukira kuti ifeyo tikhoza kudzala komanso kuthirira koma Mulungu ndi amene amakulitsa.​—1 Akor. 3:6. w20.09 11 ¶10-11

Lamlungu, September 18

Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse pakati pa gulu la owongoka mtima ndi pamsonkhano wawo.—Sal. 111:1.

Tonsefe timafuna ophunzira athu atabatizidwa. Kuti zimenezi zitheke tiziwalimbikitsa kuti azifika pamisonkhano yampingo nthawi zonse. Nthawi zambiri ophunzira amene amafika pamisonkhano akangoyamba kuphunzira ndi omwe amabatizidwa mwamsanga. Abale ndi alongo ena amafotokozera ophunzira awo kuti akapita kumisonkhano, angakamve zinthu zambiri zimene sangaziphunzire paphunziro la Baibulo. Werengani Aheberi 10: 24, 25 ndi wophunzira wanu ndipo mufotokozereni kufunika koti azifika pamisonkhano. Mungachite bwino kumufotokozera zinthu zosangalatsa zimene mwaphunzira kumisonkhano yaposachedwapa. Zimenezi zingamuthandize kuti ayambe kufika pamisonkhano kusiyana ndi kungomuitanira kuti abwere kumisonkhano. Zimene wophunzirayo angamve ndi kuona akafika koyamba pamisonkhano yathu zidzakhala zabwino kwambiri kuposa zimene anamva ndi kuona kumisonkhano ya zipembedzo zina. (1 Akor. 14:24, 25) Komanso adzakumana ndi abale ndi alongo achitsanzo chabwino chimene ayenera kutsanzira ndiponso omwe angamuthandize kuti afike pobatizidwa. w20.10 10-11 ¶14-15

Lolemba, September 19

Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye [Mulungu]?​—Yobu 36:22.

Mzimu wa Mulungu udzakuthandizani kuti muzigwiritsa ntchito zimene mwawerenga komanso kuphunzira m’Mawu a Mulungu. Muzipemphera ngati wolemba masalimo, amene ananena kuti: “Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu. Ndidzayenda m’choonadi chanu. Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” (Sal. 86:11) Choncho muyenera kupitiriza kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo ndi mabuku ena amene gulu la Yehova limatipatsa. Pochita zimenezi cholinga chanu sichiyenera kukhala kungofuna kudziwa zambiri. M’malomwake chiyenera kukhala chakuti muzikhulupirira kwambiri choonadi komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake pa moyo wanu. Mzimu wa Yehova ungakuthandizeni kuchita zimenezi. Muyeneranso kumalimbikitsa abale ndi alongo anu. (Aheb. 10:24, 25) Zimenezi n’zofunika chifukwa amenewa ndi anthu a m’banja lanu lauzimu. Muzipemphera kuti Mulungu akupatseni mzimu woyera umene ungakuthandizeni kuti muziyankha mochokera pansi pamtima mukakhala pamisonkhano komanso ngati muli ndi nkhani muziyesetsa kuikonzekera bwino. Mukamachita zimenezi mumamusonyeza Yehova ndi Mwana wake kuti mumakonda “nkhosa” zawo zamtengo wapatali. (Yoh. 21:15-17) Choncho muzimvetsera Mlangizi Wamkulu poyesetsa kudya chakudya chonse chauzimu chimene amatipatsa. w20.10 24-25 ¶15-17

Lachiwiri, September 20

Ophunzira ake onse anathawa ndi kumusiya yekha.​—Maliko 14:50.

Kodi Yesu anachita chiyani pa nthawi imene atumwi ake anafooka? Yesu atangoukitsidwa, anauza otsatira ake ena kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga [kuti ndaukitsidwa].” (Mat. 28:10a) Yesu sanasiye ophunzira akewo. Ngakhale kuti iwo anamusiya, iye anapitirizabe kuwatchula kuti “abale anga.” Mofanana ndi Yehova, Yesu anali wachifundo komanso wokhululuka. (2 Maf. 13:23) Ifenso timadera nkhawa anthu amene anasiya kulalikira. Iwo ndi abale ndi alongo athu ndipo timawakonda. Timakumbukirabe ntchito yaikulu imene anachita potumikira Yehova. Ndipo ena a iwo agwira ntchito imeneyi kwa zaka zambiri. (Aheb. 6:10) Timawasowa kwambiri abale ndi alongo amenewa. (Luka 15:4-7) Choncho tiziwalimbikitsa kuti azibwera kumisonkhano ndipo akabwera, tiziyamba ndi ifeyo kuwalandira ndi manja awiri. w20.11 6 ¶14-17

Lachitatu, September 21

Musapitirire zinthu zolembedwa.​—1 Akor. 4:6.

Taganizirani zimene Yesu anayankha pamene Yakobo ndi Yohane limodzi ndi amayi awo anamupempha zinthu zimene sunali udindo wake kupereka. Mosazengereza iye ananena kuti ndi Atate wake okha amene ayenera kusankha yemwe angakhale kudzanja lake lamanja kapena lamanzere mu Ufumu wake. (Mat. 20:20-23) Pamenepa Yesu anasonyeza kuti ankadziwa malire ake. Iye anali wodzichepetsa ndipo sanachite zinthu zimene Yehova sanamuuze kuti achite. (Yoh. 12:49) Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo chabwino cha Yesu? Timatsanzira Yesu tikamatsatira malangizo a m’Baibulo amene ali mulemba lalelori. Choncho ena akapempha malangizo, sitiyenera kuwakakamiza kutsatira maganizo athu kapena kungolankhulapo tisanaganizire bwino nkhaniyo. M’malomwake tiyenera kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo komanso m’mabuku athu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timadziwa malire athu. Timasonyezanso kudzichepetsa tikamatsatira ‘malamulo olungama’ a Wamphamvuyonse.​—Chiv. 15:3, 4. w20.08 11-12 ¶14-15

Lachinayi, September 22

Usakhale wolungama mopitirira muyezo kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri, kuopera kuti ungadzibweretsere chiwonongeko.​—Mlal. 7:16.

Kodi ndi mfundo ziti zimene muyenera kukumbukira ngati mukufuna kupereka malangizo kwa mnzanu? Musanalankhule ndi mnzanuyo, mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndikufuna kuchita zinthu ngati munthu “wolungama mopitirira muyezo”?’ Munthu wolungama mopitirira muyezo amaweruza ena pogwiritsa ntchito mfundo zake osati za Yehova ndipo sachita zinthu mwachifundo. Mutaiganizira nkhaniyo ndipo mukuonabe kuti mukuyenera kukalankhula ndi mnzanuyo, muyenera kumufotokozera momveka bwino zimene walakwitsa komanso mungagwiritse ntchito mafunso pomuthandiza kumvetsa zimene walakwitsazo. Muzionetsetsa kuti zimene mukunena n’zochokera m’Malemba ndipo muzikumbukira kuti si udindo wanu kumuweruza koma kungomuthandiza kuona mmene Yehova akumvera ndi zochita zakezo. (Aroma 14:10) Muzigwiritsa ntchito nzeru zopezeka m’Mawu a Mulungu ndipo popereka malangizo muzikhala achifundo potsanzira Yesu. (Miy. 3:5; Mat. 12:20) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti zimene timachitira ena Yehova adzatichitiranso zomwezo.​—Yak. 2:13. w20.11 21 ¶13

Lachisanu, September 23

Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.​—Yoh. 7:24.

Kodi mungakonde kuti munthu akuweruzeni potengera khungu lanu, nkhope yanu kapena thupi lanu? N’zosachita kufunsa kuti simungakonde zimenezi. Choncho n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova satiweruza potengera zimene anthu amaona. Mwachitsanzo, pamene Samueli ankayang’ana ana a Jese sankaona zimene Yehova ankaona. Yehova anauza Samueli kuti mwana wina wa Jese adzakhala mfumu ya Aisiraeli. Koma kodi anali mwana uti? Samueli ataona mwana wamkulu wa Jese dzina lake Eliyabu ananena kuti: “Mosakayikira wodzozedwa wake waonekera pamaso pa Yehova.” Eliyabu ankaoneka wolemekezeka ngati mfumu. “Koma Yehova anauza Samueli kuti: ‘Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake, pakuti ine ndamukana ameneyu.’” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova ananenanso kuti: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Sam. 16:1, 6, 7) Tingachite bwino kutsanzira Yehova pochita zinthu ndi abale ndi alongo athu. w20.04 14 ¶1; 15 ¶3

Loweruka, September 24

Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.​—Yoh. 4:35.

Tsiku lina Yesu ankadutsa m’munda womwe uyenera kuti unali ndi balere wongomera kumene. (Yoh. 4:3-6) Kunali kutatsala miyezi pafupifupi 4 kuti adzakololedwe. Koma Yesu ananena mawu amene mwina anadabwitsa anthu. Iye anati: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35, 36) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Zikuoneka kuti Yesu ankanena za ntchito yosonkhanitsa anthu ngati mbewu. Taganizirani zimene zinali zitangochitika kumene. Ayuda sankagwirizana ndi Asamariya koma Yesu analalikira kwa mayi wachisamariya ndipo anamvetsera bwino. Yesu akulankhula zokhudza kukololazi, gulu la Asamariya omwe anamva za Yesu kuchokera kwa mayi uja linali likubwera kuti lidzaphunzire zambiri. (Yoh. 4:9, 39-42) Buku lina lofotokoza za Baibulo linanena kuti: “Anthuwo ankafunitsitsa kumvetsera . . . Zimenezi zikusonyeza kuti anali ngati mbewu zofunika kukolola.” w20.04 8 ¶1-2

Lamlungu, September 25

Ndipo tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.​—Heb. 10:24.

Misonkhano imatithandiza kuti tizilalikira komanso kuphunzitsa mwaluso. Mwachitsanzo, timaphunzitsidwa mmene tingagwiritsire ntchito bwino Zinthu Zophunzitsira. Choncho, tizikonzekera bwino misonkhano. Tikakhala pamisonkhano, tizimvetsera mwatcheru. Misonkhano ikatha, tizigwiritsa ntchito maphunziro amene talandira. Tikamachita zimenezi, tidzakhala “msilikali wabwino wa Khristu Yesu.” (2 Tim. 2:3) Tilinso ndi angelo amphamvu mamiliyoni amene amatithandiza. Taganizirani zimene mngelo mmodzi yekha angakwanitse kuchita. (Yes. 37:36) Ndiye taganizirani zimene gulu la angelo amphamvu lingachite. Palibe munthu kapena chiwanda chimene chingalimbane ndi asilikali amphamvu a Yehova amenewa. Popeza Yehova ndi wamphamvu zonse, akakhala nafe timakhala amphamvu kuposa adani athu ngakhale atakhala ochuluka bwanji. (Ower. 6:16) Ndipo sitimakayikira zimenezi ngakhale pang’ono. Choncho, muzikumbukira mfundo zimenezi ngati anzanu a kuntchito, kusukulu kapena achibale anu omwe si Mboni alankhula kapena kuchita zinthu zomwe zakukhumudwitsani. Kumbukirani kuti simuli nokha pankhondoyi koma Yehova ndi amene akukutsogolerani. w21.03 29 ¶13-14

Lolemba, September 26

Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”​—1 Akor. 15:32.

N’kutheka kuti mtumwi Paulo ananena mawu opezeka pa Yesaya 22:13, amene akufotokoza maganizo omwe Aisiraeli anali nawo. M’malo molimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu, iwo ankakonda zinthu zosangalatsa. Tinganene kuti Aisiraeliwo anali ndi maganizo akuti, ‘Tisangalaliretu ndi moyo panopa chifukwa tikhoza kufa nthawi iliyonse.’ Maganizo amenewa ndi ofalanso masiku ano. Tikudziwa kuti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira ndipo zimenezi ziyenera kutithandiza kusankha bwino anthu ocheza nawo. Abale a ku Korinto ankafunika kupewa kucheza ndi anthu amene ankatsutsa zoti akufa adzauka. Pamenepa phunziro kwa ife ndi lakuti: Tikamacheza kwambiri ndi anthu amene saganizira zam’tsogolo koma amangoganizira zinthu zosangalatsa, angatisokoneze. Ngati Mkhristu weniweni atamacheza ndi anthu amenewa, angayambe kutengera maganizo ndi makhalidwe oipa. Ndipotu anthu amenewa angamuchititse kuti ayambe kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. N’chifukwa chake Paulo akutilimbikitsa kuti: “Dzukani ku tulo tanu kuti mukhale olungama ndipo musamachite tchimo.”​—1 Akor. 15:33, 34. w20.12 9 ¶3, 5-6

Lachiwiri, September 27

Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.​—1 Akor. 11:3.

Vesili likusonyeza zimene Yehova anakonza pa nkhani yotsogolera m’banja lake lakumwamba komanso lapadziko lapansi. Kukhala mutu kumaphatikizapo zinthu ziwiri izi: kukhala ndi mphamvu komanso udindo. Yehova ndi “mutu,” ndipo iye ndi amene ali ndi mphamvu zonse. Popeza amatha kupereka mphamvu komanso udindo kwa ana ake omwe akuphatikizapo angelo ndi anthu, Yehova amayembekezera kuti iwo agwiritsa ntchito bwino udindo kapena mphamvu zawo. (Aroma 14:10; Aef. 3:14, 15) Yehova wapereka kwa Yesu udindo wotsogolera mpingo, ndipo amayembekezera kuti iye azigwiritsa ntchito bwino udindo wake potitsogolera. (1 Akor. 15:27) Waperekanso kwa mwamuna udindo wotsogolera mkazi ndi ana ake. Ndiye kodi mwamuna angatani kuti akhale mutu wa banja wabwino? Choyamba, ayenera kumvetsa zimene Yehova amafuna kuti iye azichita. Amafunikanso kudziwa chifukwa chake Yehova anakonza zakuti ena azitsogolera anzawo komanso zimene angachite kuti azitsanzira Yehova ndi Yesu. N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kudziwa zimenezi? Zili choncho chifukwa Yehova anapereka udindo wotsogolera m’banja kwa mwamuna, ndipo amafuna kuti azigwiritsa ntchito udindowu moyenera.​—Luka 12:48b. w21.02 2 ¶1-3

Lachitatu, September 28

Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.​—Yes. 48:17.

Tingachite bwino kutsanzira Yehova posankha kuiwala zinthu zina. Timadziwa kuti iye amakumbukira bwino zinthu, komabe tikalapa zolakwa zathu, amatikhululukira ndipo amaiwala zomwe tamulakwirazo. (Sal. 25:7; 130:3, 4) Yehova amafunanso kuti tizichita zimenezi kwa anzathu akatipepesa pa zomwe anatilakwira. Tingasonyeze kuyamikira Mulungu kuti anatipatsa ubongo tikamaugwiritsa ntchito pomulemekeza. Anthu ena amagwiritsa ntchito ubongo wawo pochita zinthu zongodzisangalatsa. Amachita zimenezi posankha okha zomwe akuona kuti n’zoyenera ndi zosayenera. Koma ndi nzeru kuyembekezera kuti Yehova azitiuza zomwe zili zoyenera ndi zosayenera chifukwa iye ndi amene anatilenga. (Aroma 12:1, 2) Tikamatsatira mfundo zake, timakhala pamtendere. (Yes. 48:18) Timamvetsanso kuti anatilenga n’cholinga choti tizimulemekeza monga Mlengi komanso Atate wathu ndiponso kuti tizichita zinthu zomusangalatsa.​—Miy. 27:11. w20.05 23-24 ¶13-14

Lachinayi, September 29

Khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu.​—Aroma 12:10.

Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri abale ndi alongo athu? Tikamawadziwa bwino abale ndi alongo athu, zimakhala zosavuta kuti tiziwamvetsa komanso kuti tiyambe kuwakonda kwambiri. Tikhoza kukhala nawo pa ubwenzi posatengera msinkhu wawo kapena chikhalidwe chawo. Kumbukirani kuti Yonatani ankasiyana ndi Davide ndi zaka pafupifupi 30, komabe iye ankamuona ngati mnzake wa pamtima. Kodi mumpingo mwanu muli wina wake yemwe ndi wamkulu kapena wamng’ono kuposa inuyo amene akhoza kukhala mnzanu? Mukamayesetsa kuti aliyense akhale mnzanu mungasonyeze kuti ‘mumakonda gulu lonse la abale.’ (1 Pet. 2:17) Tikamayesetsa kukonda abale ndi alongo athu, kodi zikutanthauza kuti aliyense mumpingo adzakhala bwenzi lathu la pamtima? Ayi, zimenezi sizingatheke. Sikulakwa kugwirizana ndi anthu ena kuposa ena chifukwa choti mwina timakonda zinthu zofanana. Yesu anatchula atumwi ake onse kuti “mabwenzi,” koma iye ankakonda kwambiri Yohane. (Yoh. 13:23; 15:15; 20:2) Komabe si kuti Yesu ankachita naye zinthu momukondera.​—Maliko 10:35-40. w21.01 23 ¶12-13

Lachisanu, September 30

Mumaopa kwambiri milungu kuposa mmene ena amachitira.​—Mac. 17:22.

Mtumwi Paulo sanalalikire anthu amitundu ina ku Atene ngati mmene analalikirira Ayuda musunagoge. Iye ayenera kuti anadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu a ku Atenewa amakhulupirira zotani?’ Ankayang’ana kwambiri zinthu zamumzindawu kuti adziwe za miyambo yawo yachipembedzo. (Mac. 17:23) Kenako Paulo ankayesetsa kupeza mfundo za m’chipembedzo chawo zomwe zinkafanana ndi mfundo zoona za m’Malemba. Pofotokoza za Paulo, katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Popeza anali Mkhristu wa Chiyuda, ankadziwa kuti Agiriki ambiri sankalambira Mulungu ‘woona,’ yemwe Ayuda ndiponso Akhristu ankamulambira. Koma iye anayesetsa kusonyeza kuti Mulungu amene ankamulalikira kwa anthuwo sanali wachilendo kwa anthu a ku Atene.” Izi zikusonyeza kuti Paulo ankasintha uthenga wake kuti ugwirizane ndi anthu amene ankawalalikira. Iye anauza anthu a ku Atene kuti uthenga wake umachokera kwa “Mulungu Wosadziwika” yemwe iwo ankayesa kumulambira. Ngakhale kuti anthuwa sankadziwa Malemba, Paulo ankayesetsabe kuwalalikira. Iye ankawaona kuti ali ngati mbewu zofunika kukolola ndipo anasintha njira yolalikirira uthenga wabwino. Mofanana ndi Paulo, tizikhala tcheru. Tiziyesetsa kuona zinthu zimene zingatithandize kudziwa zomwe anthu am’gawo lathu amakhulupirira. Mwachitsanzo, kodi munthu wakongoletsa bwanji nyumba yake? Kodi dzina lake, zovala zake kapena mawu amene amagwiritsa ntchito zikusonyeza kuti ali m’chipembedzo chinachake? w20.04 9-10 ¶7-8

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena