October
Loweruka, October 1
“Ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti amulangize?” Koma ifeyo tili ndi maganizo a Khristu.—1 Akor. 2:16.
Tikadziwa bwino maganizo a Yesu n’kumamutsanzira timayamba kugwirizana naye kwambiri. Koma kodi tingatsanzire bwanji Yesu? Tiyeni tingokambirana njira imodzi. Yesu ankaganizira kwambiri zothandiza anthu ena osati kudzisangalatsa yekha. (Mat. 20:28; Aroma 15:1-3) Maganizo amenewa anamuthandiza kuti azichita zinthu modzipereka komanso azikhululukira anthu ena. Iye sankakhumudwa msanga anthu akalankhula zinthu zolakwika zokhudza iyeyo. (Yoh. 1:46, 47) Komanso sankasungira anthu zifukwa. (1 Tim. 1:12-14) Yesu ananena kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, “Kodi ineyo ndimatsanzira Yesu pochita zonse zimene ndingathe kuti ndizikhala mwamtendere ndi abale ndi alongo?” w20.04 24 ¶11
Lamlungu, October 2
Iwo adzayeretsa dzina langa.—Yes. 29:23.
Ngakhale kuti mukukhala m’dziko limene anthu amanyoza komanso kudetsa dzina la Mulungu, muli ndi mwayi woteteza dzina lake ndi kuuza anthu zoona zokhudza iyeyo. Mungathandize ena kudziwa kuti Yehova ndi woyera, wolungama, wabwino komanso wachikondi. Mungasonyeze kuti muli kumbali ya Ufumu wa Mulungu ndipo mungathandize ena kudziwa kuti ndi ulamuliro wake wokha umene udzabweretse mtendere m’chilengedwe chonse. (Sal. 37:9, 37; 146:5, 6, 10) Nthawi zambiri tikamaphunzira Baibulo ndi ena, timafotokoza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira ndipo zimenezi n’zoona. Komabe ngakhale kuti ndi zofunika kuphunzitsa anthu malamulo a Mulungu, cholinga chathu chachikulu ndi kuwathandiza kuti ayambe kumukonda komanso kukhala okhulupirika kwa iye. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti adziwe makhalidwe abwino a Yehova komanso kuti amudziwe kuti ndi wotani. (Yes. 63:7) Tikamaphunzitsa anthu mwa njira imeneyi, tidzakwaniritsa cholinga chathu chowathandiza kuti akhale okhulupirika kwa Yehova ndipo adzayamba kumukonda komanso kumumvera. w20.06 6 ¶16; 7 ¶19
Lolemba, October 3
Anapatsa munthu pakamwa ndani . . . ? Kodi si ine, Yehova?—Eks. 4:11.
Ubongo wathu unapangidwa modabwitsa kwambiri. Mwana akamakula m’mimba mwa mayi ake, ubongo wake umapangika motsatira dongosolo lapadera ndipo pa miniti iliyonse pamapangika maselo masauzande ambiri. Akatswiri ena amati ubongo wa munthu wamkulu umakhala ndi maselo okwana 100 biliyoni otchedwa manyuroni. Ubongo wamunthu umalemera pafupifupi kilogalamu imodzi ndi hafu, ndipo umapangidwa ndi maselo amenewa. Chimodzi mwa zinthu zomwe zimasonyeza kuti ubongo wathu ndi wogometsa ndi zimene zimachitika kuti tizilankhula. Kuti mutulutse mawu enaake, ubongo wanu umawongolera kayendedwe ka minofu pafupifupi 100 yalilime, yapakhosi, yansagwada, yapachifuwa komanso yamilomo. Kuti mawuwo akhale omveka bwino, minofuyi imafunika kuyenda mwadongosolo. Zotsatira za kafukufuku wina zimene zinatuluka mu 2019 zinasonyeza kuti ana ongobadwa kumene amatha kuzindikira mawu ena ndi ena. Izi zikugwirizana ndi zimene ochita kafukufuku ambiri amakhulupirira kuti anthufe timabadwa ndi luso lozindikira komanso kuphunzira zilankhulo. Kunena zoona, kulankhula ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. w20.05 22-23 ¶8-9
Lachiwiri, October 4
Anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.—Aheb. 11:10.
Abulahamu analolera kusiya moyo wabwino kwambiri umene anali nawo mumzinda wa Uri. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa ankayembekezera “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Aheb. 11:8-10, 16) Mzinda umene Abulahamu ankayembekezerawu ndi Ufumu wa Mulungu. Yesu Khristu komanso Akhristu odzozedwa okwana 144,000 ndi amene ali olamulira a Ufumuwu. Paulo anatchula Ufumu umenewu kuti ndi “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba.” (Aheb. 12:22; Chiv. 5:8-10; 14:1) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipempherera Ufumuwu kuti ubwere kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi ngati mmene chikuchitikira kumwamba. (Mat. 6:10) Kodi Abulahamu ankadziwa mmene Ufumu wa Mulungu udzakhalire? Ayi. Tikutero chifukwa kwa zaka zambiri nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu inali “chinsinsi chopatulika.” (Aef. 1:8-10; Akol. 1:26, 27) Koma Abulahamu ankadziwa kuti ena mwa ana ake adzakhala mafumu chifukwa Yehova anali atamulonjeza kale zimenezi.—Gen. 17:1, 2, 6. w20.08 2-3 ¶2-4
Lachitatu, October 5
Yendanibe mogwirizana ndi [Ambuye]. Khalanibe ozikika mozama mwa iye, . . . pitirizani kukula pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.—Akol. 2:6, 7.
Tiyenera kupewa ziphunzitso za anthu ampatuko. Kungochokera pamene mpingo wa Chikhristu unayamba, Satana wakhala akugwiritsa ntchito ampatuko kuti azichititsa atumiki okhulupirika a Yehova kukayikira kuti zimene amakhulupirira ndi zoona. Choncho n’zofunika kuti tizitha kusiyanitsa pakati pa zoona ndi zabodza. Adani athu akhoza kugwiritsa ntchito intaneti kapena malo ena ochezera a pa intaneti n’cholinga choti atichititse kusiya kukhulupirira Yehova komanso kukonda abale ndi alongo athu. Musamaiwale kuti Satana ndi amene amafalitsa mabodza amenewa ndipo sitiyenera kuwakhulupirira. (1 Yoh. 4:1, 6; Chiv. 12:9) Kuti Satana asafooketse chikhulupiriro chathu, tiyenera kumakhulupirira Yesu komanso kuzindikira udindo umene ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Tiyeneranso kumakhulupirira kwambiri anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito potsogolera gulu lake. (Mat. 24:45-47) Chikhulupiriro chathu chingalimbe kwambiri tikamaphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. Tikamatero, chikhulupiriro chathu chingafanane ndi mtengo umene mizu yake yalowa pansi kwambiri. Mtumwi Paulo anatchula mfundo yofanana ndi imeneyi pamene analemba mawu a mulemba laleroli. w20.07 23-24 ¶11-12
Lachinayi, October 6
Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.—1 Sam. 16:7.
Anthufe timakonda kuweruza anthu ena potengera maonekedwe awo. (Yoh. 7:24) Koma zimene timaona ndi maso athu sizingatithandize kudziwa zambiri zokhudza munthu. Mwachitsanzo, ngakhale dokotala wanzeru kwambiri sangadziwe zambiri akangoona wodwala. Iye ayenera kumvetsera mwatcheru zimene munthuyo angafotokoze zokhudza matenda amene anadwalapo kale, mmene maganizo ake alili komanso mmene akumvera m’thupi. Mwina dokotalayo akhoza kupempha kuti munthuyo akajambulidwe kuti aone mkati mwa thupi lake. Kupanda kutero, akhoza kumupatsa mankhwala olakwika. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Sitingadziwe bwino abale ndi alongo athu pongoona mmene amaonekera. Tiyenera kuyesetsa kudziwa mmene alili. N’zoona kuti sitingaone zamumtima mwa munthu. Koma n’zotheka kuchita zonse zimene tingathe pomutsanzira. Yehova amamvetsera atumiki ake, amaganizira mmene moyo wawo ulili komanso amawachitira chifundo. w20.04 14-15 ¶1-3
Lachisanu, October 7
Aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.—Aroma 12:3.
Kudzichepetsa n’kofunika kwambiri chifukwa kunyada kumachititsa kuti munthu ‘asamaganize bwino.’ Anthu onyada amakhala odzikuza komanso sachedwa kukangana ndi ena. Nthawi zambiri zimene amaganiza ndiponso kuchita zimawabweretsera mavuto komanso zimavutitsa anthu ena. Ngati anthu oterewa sangasinthe, Satana akhoza kuchititsa khungu komanso kusokoneza maganizo awo. (2 Akor. 4:4; 11:3) Munthu wodzichepetsa amakhala woganiza bwino. Iye amadziona moyenera ndipo amazindikira kuti anthu ena amamuposa m’njira zambiri. (Afil. 2:3) Amadziwanso kuti “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Pet. 5:5) Anthu amene amaganiza bwino safuna kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti adane ndi Yehova. Kuti tipitirize kukhala odzichepetsa, tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘tivule umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndi kuvala umunthu watsopano.’ Tiyenera kuphunzira zimene Yesu ankachita ndi kuyesetsa kumutsanzira mosamala kwambiri.—Akol. 3:9, 10; 1 Pet. 2:21. w20.07 7 ¶16-17
Loweruka, October 8
Thupi lomwe ndi limodzi koma lili ndi ziwalo zambiri.—1 Akor. 12:12.
Tili ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala mumpingo wa Yehova. Timakhala mwamtendere komanso mosangalala tikamalambira limodzi ndi abale ndi alongo athu. Koma kodi ndinu ofunika bwanji mumpingo? Mtumwi Paulo anayerekezera mpingo ndi thupi la munthu. Anayerekezeranso anthu amumpingo ndi ziwalo zathupi. (Aroma 12:4-8; 1 Akor. 12:12-27; Aef. 4:16) Mfundo imodzi imene tikuphunzira kuchokera m’chitsanzo cha Paulo ndi yakuti aliyense ndi wofunika kwambiri mumpingo. Paulo anayamba chitsanzo chakechi ndi mawu akuti: “Monga tilili ndi ziwalo zambiri m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi chiwalo cha mnzake.” (Aroma 12:4, 5) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamenepa? Ankatanthauza kuti aliyense amakhala ndi zochita zosiyana ndi za mnzake mumpingo, koma tonsefe ndi amtengo wapatali kwa Yehova. w20.08 20 ¶1-2; 21 ¶4
Lamlungu, October 9
Yehova anamufunsa kuti, “Ukam’pusitsa motani?”—1 Maf. 22:21.
Makolo, kodi mungatsanzire bwanji Yehova pankhani ya kudzichepetsa? Ngati n’koyenera, muzifunsa ana anu mmene mungachitire zinthu zinazake. Ndiye akapereka maganizo othandiza, muziwatsatira. Yehova amasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa pokhala woleza mtima ngakhale pamene atumiki ake akukayikira zimene wasankha kuchita. Iye anamvetsera pamene Abulahamu ankafotokoza kuti sakanachita bwino kuwononga mzinda wa Sodomu ndi Gomora. (Gen. 18:22-33) Kumbukiraninso mmene Yehova anachitira zinthu ndi Sara, mkazi wa Abulahamu. Sanakhumudwe kapena kukwiya pamene Sara anaseka atamva lonjezo loti adzakhala ndi pakati ngakhale kuti anali wokalamba. (Gen. 18:10-14) M’malomwake Yehova anamulemekeza. Makolo komanso Akulu, kodi mungaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yehova? Kodi mumatani ngati ana anu kapena anthu ena mumpingo sanagwirizane ndi zimene mwasankha? Kodi nthawi zonse mumangodziikira kumbuyo kuti zosankha zanuzo ndiye zolondola? Kapena mumayesetsa kumvetsera maganizo awo? Zinthu zimayenda bwino m’banja komanso mumpingo ngati anthu amene akutsogolera amatsanzira Yehova. w20.08 10 ¶7-9
Lolemba, October 10
Mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.—2 Akor. 12:9.
Titangoyamba kumene kuphunzira choonadi, tinkafunitsitsa kuti anthu ena azitithandiza chifukwa tinkadziwa kuti sitidziwa zambiri. (1 Akor. 3:1, 2) Nanga bwanji panopa? N’kutheka kuti takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri ndipo tikudziwa zinthu zochuluka. Nthawi zina zimenezi zingachititse kuti tizivutika kulola kuti ena atithandize, makamaka ngati munthu amene akutithandizayo wangophunzira kumene choonadi. Komatu nthawi zambiri Yehova amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu kuti atilimbikitse. (Aroma 1:11, 12) Choncho ngati tikufuna kuti Yehova azitipatsa mphamvu, tiyenera kulola kuti abale ndi alongo athu azitithandiza. Tiyenera kuzindikira kuti mphamvu, maphunziro, chuma komanso kumene munthu anachokera sizingamuthandize kuchita zinthu zabwino. Chofunika kwambiri ndi kudzichepetsa komanso kudalira Yehova. Tiyeni tiziyesetsa (1) kudalira Yehova, (2) kuphunzira kuchokera kwa anthu otchulidwa m’Baibulo komanso (3) kulola kuti Akhristu anzathu azitithandiza. Tikatero, Yehova adzatipatsa mphamvu ngakhale zitakhala kuti timadziona kuti ndife ofooka kapena kuti opanda mphamvu. w20.07 14 ¶2; 19 ¶18-19
Lachiwiri, October 11
Aliyense wa inu apitirize kuonetsa khama limene anali nalo poyamba . . . kuti musakhale aulesi, koma mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.—Aheb. 6:11, 12.
Nthawi zina tingavutike kukhala oleza mtima tikamalalikira achibale athu. Zikatere, mfundo imene imapezeka pa Mlaliki 3:1, 7 ingatithandize. Lembali limati pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” Khalidwe lathu labwino lingathandize achibale athu kumvetsera uthenga wabwino. Komabe nthawi zonse tingachite bwino kukhala okonzeka kuti tiziwauza zokhudza Yehova. (1 Pet. 3:1, 2) Tiyenera kumagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa mwakhama koma tikamachita zimenezi tizilezera mtima anthu onse kuphatikizapo achibale athu. Tingaphunzirenso kukhala oleza mtima kuchokera kwa anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo komanso kwa atumiki okhulupirika amasiku ano. Habakuku ankafunitsitsa zinthu zoipa zitatha, koma anasonyeza kuti anali woleza mtima pamene ananena kuti: “Ine ndidzaimabe pamalo a mlonda.” (Hab. 2:1) Mtumwi Paulo ananena kuti ankafunitsitsa ‘atamaliza utumiki wake.’ Komabe, anapitiriza “kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino” moleza mtima.—Mac. 20:24. w20.09 11-12 ¶12-14
Lachitatu, October 12
Kukhala wolingana ndi Mulungu [Yesu] sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.—Afil. 2:6.
Yesu ndi wachiwiri kwa Yehova, komatu sadziganizira kwambiri kuposa mmene ayenera kudziganizira. Potsanzira Yesu, atumiki a Yehova amene ndi odzichepetsa amasonyeza chikondi. Zimenezi zimathandiza kuti azidziwika kuti ndi atumiki a Mulungu. (Luka 9:48; Yoh. 13:35) Tiyerekeze kuti mukuona kuti mumpingo muli mavuto enaake ndipo akulu sakuwasamalira bwino. Kodi mungatani? M’malo momangodandaula, mungasonyeze kuti ndinu odzichepetsa mukamachita zinthu mogwirizana ndi amene akutitsogolera. (Aheb. 13:17) Kuti muthe kuchita zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Kodi mavuto amene ndikuwaganizirawa ndi aakulu kwambiri moti akufunikadi kukonzedwa? Kodi ino ndi nthawi yoyenera kukonza zimenezi? Kodi ndi udindo wanga kukonza zimenezi? Kodi cholinga changa ndi kufuna kulimbikitsa mtendere mumpingo kapena ndikungofuna kutchuka?’ Yehova amaona kuti kukhala wodzichepetsa ndi kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi luso linalake. Amaonanso kuti kuchita zinthu mogwirizana ndi kofunika kwambiri kuposa kuchita zinthu mwaluso. Choncho muziyesetsa kutumikira Yehova modzichepetsa. Mukamachita zimenezi mudzathandiza kuti anthu mumpingo azigwirizana.—Aef. 4:2, 3. w20.07 4-5 ¶9-11
Lachinayi, October 13
Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga.”—Mat. 28:10.
Yesu ankayamikira kwambiri zimene akazi okonda Mulungu ankachita pomutumikira ndi “chuma chawo.” (Luka 8:1-3) Iye anawalola kuti azimutumikira komanso ankawaphunzitsa choonadi chokhudza cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, anawauza kuti adzaphedwa kenako adzaukitsidwa. (Luka 24:5-8) Iye anawauza akaziwa monganso mmene anachitira ndi atumwi, kuti adzakumana ndi mayesero. (Maliko 9:30-32; 10:32-34) N’zochititsa chidwi kuti atumwi ena atathawa pamene Yesu ankagwidwa, ena mwa akazi omwe ankamutumikirawa anali pambali pake ndipo anamuona akufa mozunzika pamtengo. (Mat. 26:56; Maliko 15:40, 41) Akazi ndi amene anayamba kudziwa kuti iye waukitsidwa. Kenako anatuma akaziwo kuti akauze atumwi kuti waukitsidwa. (Mat. 28:5, 9, 10) Komanso zikuoneka kuti pa Pentekosite mu 33 C.E., akazi ena analipo pamene Mulungu ankapereka mzimu woyera. Onse amene analipo anapatsidwa mphatso yolankhula zinenero zina ndipo ankauza ena “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Mac. 1:14; 2:2-4, 11. w20.09 23 ¶11-12
Lachisanu, October 14
Uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.
Kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu ndi ntchito yopulumutsa miyoyo. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa Yesu popereka lamulo lopezeka pa Mateyu 28:19, 20, ananena kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.” Kodi kubatizidwa n’kofunika bwanji? Munthu kuti adzapeze moyo wosatha ayenera kubatizidwa. Munthu amene akufuna kubatizidwa ayenera kukhulupirira kuti adzapeza moyo wosatha chifukwa chakuti Yesu anatifera ndipo anaukitsidwa. N’chifukwa chake mtumwi Petulo anauza Akhristu anzake kuti: ‘Ubatizo ukupulumutsanso inuyo tsopano mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.’ (1 Pet. 3:21) Choncho munthu akabatizidwa, amayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha. Kuti tithandize anthu kukhala ophunzira a Yesu tiyenera kukhala ndi “luso la kuphunzitsa.” (2 Tim. 4:1, 2) N’chifukwa chiyani timafunika kukhala ndi luso? Chifukwa chakuti Yesu anatilamula kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse.” Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti “pitiriza” kugwira ntchito imeneyi, “chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.” w20.10 14 ¶1-2
Loweruka, October 15
Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.—Luka 5:10.
Mtumwi Petulo anayamba kukonda ntchito yosodza anthu. Yehova anamuthandiza kwambiri kuti azigwira bwino ntchito imeneyi. (Mac. 2:14, 41) Timalalikira chifukwa timakonda Yehova ndipo chimenechi n’chifukwa chachikulu chomwe timagwirira ntchito imeneyi. Kukonda Yehova kumatithandiza kuti tizigwirabe ntchito yolalikira ngakhale zitakhala kuti tikukayikira kuti sitingakwanitse. Pamene Yesu ankauza Petulo kuti akhale msodzi wa anthu anamuuza kuti: “Usachite mantha.” (Luka 5:8-11) Pamenepa si kuti Petulo ankachita mantha ndi zimene zingachitike ngati atakhala wophunzira wa Yesu. M’malomwake, iye anadabwa kwambiri ndi kuchuluka kwa nsomba zimene Yesu anawathandiza kuti agwire. Iye anadziwa kuti Yesu wawathandiza kugwira nsombazo mozizwitsa ndipo zimenezi zinachititsa kuti azidziona kuti sanali woyenera kugwira ntchito ndi Yesu. Mofanana ndi Petulo, nanunso mukhoza kumachita mantha. Mwina mungamaone kuti simungakwanitse kuchita zonse zimene ophunzira a Khristu akuyenera kuchita. Ngati ndi choncho, yesetsani kuti muzikonda kwambiri Yehova, Yesu komanso anthu ena. Mukatero, mudzakhala ofunitsitsa kukhala msodzi wa anthu.—Mat. 22:37, 39; Yoh. 14:15. w20.09 3 ¶4-5
Lamlungu, October 16
Choncho pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. . . . ndi kuwaphunzitsa.—Mat. 28:19, 20.
Timasangalala kugwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso ndalama zathu pofufuza anthu amene ali ndi “maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.” (Mac. 13:48) Tikamachita zimenezi, timakhala tikutengera chitsanzo cha Yesu. Paja iye anati: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yoh. 4:34; 17:4) Ifenso tikufunitsitsa kutsiriza ntchito imene Yesu anatipatsa. (Yoh. 20:21) Ndipo tikufuna kuti enanso kuphatikizapo amene anasiya kulalikira, apitirize kugwira nafe ntchitoyi. (Mat. 24:13) Kunena zoona, si zophweka kugwira ntchito imene Yesu anatilamula. Komabe sitikhala tokha pogwira ntchitoyi chifukwa Yesu analonjeza kuti adzakhala nafe. Tikamagwira ntchito yophunzitsa anthu timakhala “antchito anzake a Mulungu” komanso “otsatira Khristu.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 2:17) Choncho, tingakwanitse kugwira ntchito imeneyi. Timasangalala kugwira ntchito imeneyi ndipo timaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza ena kuti azichitanso chimodzimodzi.—Afil.4:13. w20.11 7 ¶19-20
Lolemba, October 17
Yesu anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.—Luka 2:52.
Nthawi zambiri, zimene makolo amasankha kuchita zimakhudza ana awo kwa nthawi yayitali. Ngati makolo sangasankhe zinthu mwanzeru, zingabweretse mavuto kwa ana awo. Koma akasankha zinthu mwanzeru amathandiza anawo kuti akhale ndi moyo wabwino komanso osangalala. Komabe anawo paokha ayeneranso kusankha zinthu mwanzeru. Chinthu chanzeru chimene aliyense angasankhe ndi kutumikira Atate wathu wachikondi Yehova. (Sal. 73:28) Makolo a Yesu ankathandiza ana awo kutumikira Yehova ndipo zimene ankasankha zinasonyeza kuti ankaona kuti kutumikira Yehova ndi kofunika kwambiri pa moyo wawo. (Luka 2:40, 41, 52) Yesu nayenso ankasankha zinthu mwanzeru ndipo zimenezi zinkamuthandiza kuti azichita zimene Yehova amafuna. (Mat. 4:1-10) Yesu atakula anali munthu wokoma mtima, wokhulupirika komanso wolimba mtima. Makolo onse amene amakonda Yehova angasangalale kukhala ndi mwana ngati ameneyu. w20.10 26 ¶1-2
Lachiwiri, October 18
Maso ako aziyang’ana patsogolo.—Miy. 4:25.
Taganizirani zitsanzo zitatu izi. Mlongo wachikulire akukumbukira zinthu zimene ankasangalala nazo m’mbuyomo. Ngakhale kuti akukumana ndi mavuto iye akuchita zonse zimene angathe potumikira Yehova. (1 Akor. 15:58) Tsiku lililonse amaganizira ali m’dziko latsopano limodzi ndi anzake komanso achibale ake. Mlongo wina akukumbukira zinthu zokhumudwitsa zimene munthu wina mumpingo anamuchitira, koma anasankha kuti amukhululukire. (Akol. 3:13) M’bale wina akukumbukira zinthu zimene analakwitsa m’mbuyomo, koma panopa akuyetsetsa kuti azichita zonse zomwe angathe kuti azitumikira Yehova mokhulupirika. (Sal. 51:10) Kodi Akhristu atatuwa akufanana bwanji? Onse akukumbukira zinthu zimene zinawachitikira m’mbuyomo komabe si kuti nthawi zonse amangoganizira zinthu zimenezo. M’malomwake iwo ‘akuyang’ana patsogolo.’ N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Munthu amene akuyenda n’kumayang’ana kumbuyo, akhoza kupatuka panjira mosavuta. Zimenezi n’zofanana ndi zimene zingachitike pamene tikutumikira Yehova. Sitingathe kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse ngati nthawi zonse timaganizira zinthu zimene zinachitika kapena zinthu zimene tinachita m’mbuyo.—Luka 9:62. w20.11 24 ¶1-3
Lachitatu, October 19
Anayamba kumuderera.—1 Sam. 17:42.
Goliati yemwe anali msilikali wamphamvu ankaona kuti Davide ndi wopanda mphamvu. Goliati anali wamphamvu, anali ndi zida komanso anali wodziwa kumenya nkhondo. Pamene Davide anali kamnyamata komwe kanali kasanamenyepo nkhondo ndipo ankaoneka ngati alibe zida zokwanira. Koma Davide anadalira Yehova kuti amupatse mphamvu ndipo anagonjetsa mdani wakeyo. (1 Sam. 17:41-45, 50) Davide anakumananso ndi vuto lina lomwe likanamuchititsa kuti azidziona kuti ndi wofooka komanso wopanda mphamvu. Iye ankatumikira mokhulupirika Sauli, yemwe anali mfumu ya Isiraeli. Poyamba Sauli ankalemekeza Davide. Koma kenako, kunyada kunamuchititsa kuti azichitira nsanje Davide, moti anayamba kumuchitira zoipa komanso ankafuna kumupha. (1 Sam. 18:6-9, 29; 19:9-11) Ngakhale Sauli ankamuchitira zinthu zopanda chilungamo, Davide anapitiriza kumulemekeza chifukwa ankadziwa kuti Sauliyo ndi mfumu yosankhidwa ndi Yehova. (1 Sam. 24:6) Davide ankadalira Yehova kuti amupatse mphamvu kuti athe kupirira mayesero ovutawa.—Sal. 18:1, timawu tapamwamba. w20.07 17 ¶11-13
Lachinayi, October 20
M’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwera idzayamba kukankhana ndi [mfumu ya kumpoto].—Dan. 11:40.
Mbali yaikulu ya ulosi wonena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera yakwaniritsidwa kale ndipo sitikukayikira kuti mbali yotsala ikwaniritsidwanso. Kuti timvetse bwino ulosi wa mu Danieli chaputala 11 tiyenera kudziwa kuti ulosiwu umanena za olamulira komanso maboma okhawo omwe akhala akulimbana ndi anthu a Mulungu. Anthu a Mulungu ndi ochepa kwambiri tikayerekeza ndi anthu ena onse padzikoli, ndiye n’chifukwa chiyani mabomawa amalimbana nawo? Amalimbana nawo chifukwa cholinga chachikulu cha Satana ndi onse omwe ali kumbali yake n’chofuna kuthana ndi onse omwe akutumikira Yehova ndi Yesu. (Gen. 3:15; Chiv. 11:7; 12:17) Tiyenera kudziwanso kuti ulosi womwe Danieli analemba uyenera kugwirizana ndi maulosi ena a m’Baibulo. Choncho kuonanso zomwe Malemba ena amanena kungatithandize kumvetsa bwino ulosiwu. w20.05 2 ¶1-2
Lachisanu, October 21
Kodi akufa adzaukitsidwa motani? Inde, kodi iwo adzauka ndi thupi lotani?—1 Akor. 15:35.
Anthu ambiri masiku ano amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Koma kodi Baibulo limati chiyani? Munthu akamwalira, thupi lake limawola. Koma amene analenga chilengedwe chonsechi, angathe kuukitsa munthu ameneyo n’kumupatsa thupi loyenerera. (Gen. 1:1; 2:7) Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo posonyeza kuti Mulungu sadzafunika kuukitsa munthu ndi thupi limene anali nalo poyamba. Taganizirani za njere kapena “mbewu chabe”. Njere ikadzalidwa munthaka imamera n’kukhala mbewu. Mbewu imene yamerayo imakhala yosiyana kwambiri ndi njere imene tinadzala ija. Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chimenechi posonyeza kuti Mlengi angapereke “thupi monga mwa kufuna kwake.” Iye ananenanso kuti “palinso matupi akumwamba, ndi matupi apadziko lapansi.” Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa? Iye ankatanthauza kuti padzikoli tili ndi matupi a nyama koma kumwamba kuli matupi auzimu ngati amene angelo ali nawo.—1 Akor. 15:36-41. w20.12 9-10 ¶7-9
Loweruka, October 22
Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti? Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti?—Sal. 13:2.
Tonsefe timafuna tizikhala mosatekeseka komanso mwamtendere. Palibe amene amafuna kuti azida nkhawa. Komabe nthawi zina tingakumane ndi zinthu zimene zingatidetse nkhawa. Zimenezi zingatichititse kufunsa funso lofanana ndi limene Mfumu Davide anafunsa mulemba laleroli. Pali zinthu zambiri zimene zingatichititse kuti tizida nkhawa, ndipo zina mwa zimenezi sitingaziletse kuti zisamachitike. Mwachitsanzo, chaka chilichonse sitingaletse kukwera mitengo kwa zinthu monga chakudya, zovala kapena nyumba. Komanso sitingadziwiretu kuti anzathu a kuntchito kapena kusukulu adzatiyesa kangati kuti tikhale osakhulupirika, kapena kuti tichite makhalidwe oipa. Sitingaletsenso anthu a m’dera limene timakhala kuti asamachite zinthu zophwanya malamulo. Timakumana ndi mavuto amenewa chifukwa tikukhala m’dziko limene anthu ake satsatira mfundo za m’Baibulo. Satana, yemwe ndi mulungu wa nthawi ino, amadziwa kuti “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino” zingachititse anthu ena kusiya kutumikira Mulungu. (Mat. 13:22; 1 Yoh. 5:19) Choncho n’zosadabwitsa kuti m’dzikoli muli mavuto ambiri amene amachititsa kuti anthu azida nkhawa. w21.01 2 ¶1, 3
Lamlungu, October 23
Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu sadzalandira moyo wosatha.—1 Yoh. 3:15.
Mtumwi Yohane anatilimbikitsa kuti tisamadane ndi abale ndi alongo athu. Ngati sitingatsatire malangizo amenewa, zingachititse kuti Satana azitigwiritsa ntchito. (1 Yoh. 2:11) Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso ena chakumapeto kwa nthawi ya atumwi. Satana anayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti atumiki a Mulungu azidana komanso kuti agawikane. Pa nthawi imene Yohane ankalemba makalata ake, anthu ena amene ankachita zinthu ngati Satana, anali atalowa mumpingo. Mwachitsanzo, mumpingo wina, Diotirefe anachititsa kuti anthu asamagwirizane. (3 Yoh. 9, 10) Iye sankalemekeza akulu omwe bungwe lolamulira linkawatumiza kuti aziyendera mipingo. Anafika mpaka pochotsa mumpingo aliyense amene ankalandira anthu amene iye ankadana nawo. Zimenezitu zinali zoipa kwambiri. Masiku anonso Satana akuyesetsa kuchititsa atumiki a Mulungu kuti asamagwirizane. Choncho, tisalole kuti tizidana ndi abale athu kapena kusiya kuwathandiza. w21.01 11 ¶14
Lolemba, October 24
Zikamaliza kuchitira umboni wawo, . . . chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa ndi kuzipha.—Chiv. 11:7.
Pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse maboma a Germany ndi Britain anazunza anthu a Mulungu omwe ankakana kumenya nawo nkhondo. Ndipo boma la United States linamanga anthu amene ankatsogolera ntchito yolalikira. Zimenezi zinakwaniritsa ulosi wa pa Chivumbulutso 11:7-10. M’ma 1930, makamaka pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, mfumu ya kumpoto inazunza kwambiri anthu a Mulungu. Chipani cha Nazi chitayamba kulamulira dziko la Germany, Hitler ndi otsatira ake analetsa ntchito ya anthu a Mulungu. Mfumu ya kumpotoyi inapha anthu a Yehova pafupifupi 1,500 ndipo enanso ambiri inawatumiza kundende zozunzirako anthu. Danieli anali ataneneratu kuti zimenezi zidzachitika. Anati mfumu ya kumpoto ‘idzaipitsa malo opatulika’ ndiponso ‘idzachotsa nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse.’ Mfumuyi inachita izi poletsa ntchito yolalikira yomwe atumiki a Mulungu ankagwira. (Dan. 11:30b, 31a) Ngakhale Hitler yemwe anali mtsogoleri wadzikolo, anafika polumbira kuti adzapha anthu onse a Mulungu m’dziko la Germany. w20.05 6 ¶12-13
Lachiwiri, October 25
Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.—Aroma 12:10.
Tikamakonda kwambiri abale ndi alongo athu, timathandiza kuti mumpingo musakhale mpikisano. Kumbukirani kuti Yonatani sanachitire nsanje Davide kapena kumuona monga munthu amene akulimbirana naye mpando wachifumu. (1 Sam. 20:42) Tonsefe tingathe kutsanzira Yonatani. Musamachitire nsanje abale ndi alongo anu chifukwa cha luso limene ali nalo, koma muzichita zinthu modzichepetsa “ndi kuona ena kukhala okuposani.” (Afil. 2:3) Muzikumbukira kuti aliyense wa ife akhoza kuchita zinazake zothandiza mumpingo. Tikakhala odzichepetsa tidzaona zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita ndipo tingaphunzire zambiri pa chitsanzo chawo chokhalabe okhulupirika. (1 Akor. 12:21-25) Tikamakondana kwambiri zimathandiza kuti tizisangalala potumikira Yehova mogwirizana. Timasonyeza kuti ndife ophunzira a Yesu ndipo zimenezi zimachititsa anthu a maganizo abwino kuti ayambe kutumikira Yehova. Koposa zonse timalemekeza Yehova yemwe ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.”—2 Akor. 1:3. w21.01 24 ¶14; 25 ¶16
Lachitatu, October 26
Popeza simuli mbali ya dzikoli, . . . dziko likudana nanu.—Yoh. 15:19.
Masiku ano, anthu ena amanyoza a Mboni za Yehova chifukwa amawaona ngati anthu opanda nzeru komanso achabechabe. Amationa choncho chifukwa timachita zinthu mosiyana ndi anthu ena. Timayesetsa kukhala odzichepetsa, ofatsa komanso omvera. Koma anthu a m’dzikoli amalemekeza anthu onyada, odzikweza komanso osamvera. Ifeyo sitichita nawo zandale ndiponso sitimenya nawo nkhondo. Popeza timachita zosiyana ndi zimene anthu a m’dzikoli amachita, amationa ngati otsalira. (Aroma 12:2) Ngakhale anthu a m’dzikoli amationa ngati otsalira, Yehova amatigwiritsa ntchito pochita zinthu zazikulu. Mwachitsanzo, panopa Yehova amatithandiza kugwira ntchito yolalikira yomwe ikugwiridwa kuposa kale lonse. Atumiki a Yehova masiku ano amamasulira komanso kufalitsa magazini m’zinenero zambirimbiri ndipo amagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu mamiliyoni kuti asinthe makhalidwe awo. Zonsezi zimatheka chifukwa cha Yehova. w20.07 15 ¶5-6
Lachinayi, October 27
Ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.—Yoh. 14:31.
Yesu amagonjera Yehova, koma si kuti amachita zimenezi chifukwa chakuti alibe nzeru kapena luso. Ndipotu ndi munthu wanzeru zambiri yekha amene angaphunzitse zomveka komanso zosavuta kumva ngati mmene Yesu ankachitira. (Yoh. 7:45, 46) Yehova ankadziwa luso limene Yesu anali nalo, moti analola kugwira naye ntchito pamene ankalenga zinthu zonse. (Miy. 8:30; Aheb. 1:2-4) Ndipo Yesu ataukitsidwa, Yehova anamupatsa ‘ulamuliro wonse, kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mat. 28:18) Ngakhale kuti Yesu ali ndi luso komanso nzeru, iye amadalirabe Yehova kuti azimutsogolera. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Amachita zimenezi chifukwa chakuti iye amakonda Atate. Amuna ayenera kutengera chitsanzo cha Yesuchi. Yehova sanakonze zoti akazi azigonjera amuna awo chifukwa chakuti amawaona kuti ndi otsika poyerekeza ndi amuna. Umboni wa zimenezi ndi wakuti iye anasankha akazi ena kuti akalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. (Agal. 3:26-29) Yehova anasonyeza kuti amadalira Mwana wake pomupatsa ulamuliro. Mofanana ndi zimenezi, mwamuna wanzeru amapatsa mkazi wake mphamvu yotha kuchita zinthu zina. w21.02 11 ¶13-14
Lachisanu, October 28
Anthu amene anapirira timawatcha odala.—Yak. 5:11.
Mawu a Mulungu ali ngati galasi ndipo amatithandiza kudziwa zimene tiyenera kukonza komanso mmene tingachitire zimenezi. (Yak. 1:23-25) Mwachitsanzo, pambuyo pophunzira Mawu a Mulungu tikhoza kuzindikira kuti tikufunika kukhala oleza mtima. Yehova angatithandize kuti tizichita zinthu modekha anthu akatikhumudwitsa kapena tikakumana ndi mavuto enaake. Kuchita zinthu modekha kungathandize kuti tithe kulimbana ndi mavuto amene takumana nawo. Izi zili choncho chifukwa timachita zinthu moganiza bwino ndipo timasankha zochita mwanzeru. (Yak. 3:13) Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizilidziwa bwino Baibulo. Nthawi zina timaphunzira zinthu zoyenera kupewa tikalakwitsa zinazake. Komatu imeneyi si njira yabwino yophunzirira zinthu. Munthu wanzeru amaphunzira pa zimene ena anachita bwino kapena zimene analakwitsa. N’chifukwa chake Yakobo anatilimbikitsa kuganizira zitsanzo za anthu a m’Baibulo monga Abulahamu, Rahabi, Yobu komanso Eliya. (Yak. 2:21-26; 5:10, 11, 17, 18) Atumiki a Yehova okhulupirikawa anapirira mayesero amene akanawachititsa kuti asamasangalale. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti nafenso Yehova angatithandize kuti tizipirira mosangalala mayesero amene tingakumane nawo. w21.02 29-30 ¶12-13
Loweruka, October 29
Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana, ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.—Miy. 20:18.
Paphunziro la Baibulo, mwiniwake wa phunzirolo ndi amene amakhala ndi udindo wothandiza wophunzirayo kumvetsa mfundo za m’Mawu a Mulungu. Choncho wina akakupemphani kuti mumuperekeze kuphunziro lake, muziona kuti wakutengani kuti mukamuthandize. (Mlal. 4:9, 10) Ndiye kodi mungatani kuti mukathandize kuti phunzirolo likakhale lopindulitsa? Muzikonzekera. Choyamba, muzifunsa mphunzitsiyo kuti akuuzeni zina ndi zina zokhudza wophunzirayo. Kodi mbiri ya wophunzirayo ndi yotani? Kodi mukaphunzira naye mutu uti? Kodi ndi mfundo zazikulu ziti zimene mukufuna mukamuphunzitse? Kodi pali zinazake zimene mukufuna kuti ndikanene kapena ndisakanene pamene tikuphunzira naye? Kodi ndingakalimbikitse bwanji wophunzirayo kuti apite patsogolo? Si kuti mphunzitsiyo angakufotokozereni nkhani zachinsinsi zokhudza wophunzirayo komabe zimene angakufotokozerenizo zingakuthandizeni kwambiri. Mmishonale wina dzina lake Joy anati: “Kuchita zimenezi kumathandiza amene ndayenda nayeyo kuti azisonyeza chidwi kwa wophunzirayo komanso kudziwiratu zomwe angalankhule paphunzirolo.” w21.03 9 ¶5-6
Lamlungu, October 30
Ngati dziko likudana nanu, mukudziwa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.—Yoh. 15:18.
Nthawi zina anthu amadana nafe chifukwa timamvera mfundo zolungama za Mulungu. Mfundo zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi zomwe anthu a m’dzikoli amatsatira pa nkhani ya zabwino ndi zoipa. Mwachitsanzo, anthu ambiri masiku ano amavomereza makhalidwe oipa kwambiri ofanana ndi amene anachititsa kuti Mulungu awononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora. (Yuda 7) Choncho, popeza timatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani yokhudza makhalidwe amenewo, anthu ambiri amatinyoza komanso amatinena kuti ndife amakani. (1 Pet. 4:3, 4) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira anthu ena akamadana nafe komanso akamatinyoza? Tiyenera kumakhulupirira kwambiri kuti Yehova atithandiza. Mofanana ndi chishango, chikhulupiriro chathu chingathe ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aef. 6:16) Komabe chikhulupiriro pachokha sichokwanira. Timafunikanso kukhala ndi chikondi. N’chifukwa chiyani? Chifukwa pajatu chikondi “sichikwiya.” Icho chimakwirira komanso kupirira zinthu zonse zokhumudwitsa. (1 Akor. 13:4-7, 13) Kukonda Yehova, Akhristu anzathu, ngakhalenso adani athu, kungatithandize kupirira ena akamadana nafe. w21.03 20-21 ¶3-4
Lolemba, October 31
Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.—Mlal. 7:9.
Nthawi zina tingasonyeze kuti timakonda abale ndi alongo athu chifukwa cha zimene sitichita. Mwachitsanzo, tingasonyeze kuti timawakonda ngati sitikhumudwa msanga chifukwa cha zimene alankhula. Taganizirani zimene zinachitika pa nthawi ina, chakumapeto kwa moyo wa Yesu ali padziko lapansili. Iye anauza ophunzira ake kuti angapeze moyo ngati atadya mnofu wake komanso kumwa magazi ake. (Yoh. 6:53-57) Zimene ananenazi zinakhumudwitsa ophunzira ake ambiri ndipo anasiya kumutsatira. Koma anzake a pamtima, sanamusiye koma anapitirizabe kumutsatira mokhulupirika. Nawonso sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza ndipo ayenera kuti anadabwa ndi mawu amenewa. Koma anzake a Yesu okhulupirikawa sanaganize kuti zimene Yesu ananenazi ndi zolakwika ndipo sanakhumudwe nazo. M’malomwake, iwo anamukhulupirira chifukwa ankadziwa kuti nthawi zonse ankalankhula zoona. (Yoh. 6:60, 66-69) Choncho ndi bwino kuti ifenso tisamafulumire kukhumudwa ndi zimene anzathu alankhula koma tiziwalola kuti atifotokozere zomwe akutanthauza.—Miy. 18:13. w21.01 11 ¶13