Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es22 tsamba 108-118
  • November

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • November
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
  • Timitu
  • Lachiwiri, November 1
  • Lachitatu, November 2
  • Lachinayi, November 3
  • Lachisanu, November 4
  • Loweruka, November 5
  • Lamlungu, November 6
  • Lolemba, November 7
  • Lachiwiri, November 8
  • Lachitatu, November 9
  • Lachinayi, November 10
  • Lachisanu, November 11
  • Loweruka, November 12
  • Lamlungu, November 13
  • Lolemba, November 14
  • Lachiwiri, November 15
  • Lachitatu, November 16
  • Lachinayi, November 17
  • Lachisanu, November 18
  • Loweruka, November 19
  • Lamlungu, November 20
  • Lolemba, November 21
  • Lachiwiri, November 22
  • Lachitatu, November 23
  • Lachinayi, November 24
  • Lachisanu, November 25
  • Loweruka, November 26
  • Lamlungu, November 27
  • Lolemba, November 28
  • Lachiwiri, November 29
  • Lachitatu, November 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2022
es22 tsamba 108-118

November

Lachiwiri, November 1

Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.​—Miy. 18:13.

Popeza sitikudziwa zonse zokhudza Yona, tikhoza kuganiza kuti anali wosadalirika kapenanso wosakhulupirika. Iye analamulidwa ndi Yehova kuti akalalikire uthenga wachiweruzo ku Nineve. Koma m’malo momvera, ‘anathawa Yehova’ n’kukwera chombo chopita kutali ndi Nineve.’ (Yona 1:1-3) Mukanakhala inuyo, kodi mukanamupatsa Yona mwayi wina woti achite zimene munamuuzazo? Mwina ayi. Koma Yehova anaona kuti ndi woyenera kumupatsa mwayi wina. (Yona 3:1, 2) Yona anasonyeza mmene analili mu pemphero lina limene anapereka. (Yona 2:1, 2, 9) N’zosakayikitsa kuti anapereka mapemphero ambirimbiri, koma pemphero limeneli limatithandiza kuti tisamangomuona kuti ndi munthu amene anathawa ntchito. Mawu am’pempheroli amasonyeza kuti anali wodzichepetsa, woyamikira komanso wofunitsitsa kumvera Yehova. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yehova sanangoona zomwe Yona analakwitsa, koma anayankha pemphero lake n’kupitiriza kumugwiritsa ntchito monga mneneri. Zimenezi zikusonyeza kuti akulu amafunika kuti ‘azimvetsetsa’ nkhani yonse asanapereke malangizo. w20.04 15 ¶4-6

Lachitatu, November 2

[Paulo] anakambirana nawo mfundo za m’Malemba. Iye anali kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa.​—Mac.17: 2, 3.

Akhristu a munthawi ya atumwi ankakhulupirira ziphunzitso za Chikhristu ndipo ankadalira mzimu woyera kuti uwathandize kumvetsa Mawu a Mulungu. Iwo anafufuza kuti atsimikizire kuti ziphunzitsozi zinalidi zochokera m’Malemba. (Mac. 17:11,12; Aheb. 5:14) Chikhulupiriro chawo sichinkangodalira mmene ankamvera mumtima mwawo ndipo sankatumikira Yehova chifukwa choti ankangosangalala kusonkhana ndi okhulupirira anzawo. M’malomwake anali ndi chikhulupiriro chifukwa choti ankayesetsa “kumudziwa Mulungu molondola.” (Akol. 1:9,10) Mfundo za choonadi cha m’Mawu a Mulungu sizisintha. (Sal. 119:160) Mwachitsanzo, mfundozi sizisintha ngakhale wokhulupirira mnzathu atikhumudwitse kapena achite tchimo lalikulu. Ndiponso sizisintha tikakumana ndi mavuto. Choncho tiziyesetsa kudziwa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kutsimikizira kuti ndi zoona. Tikamalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi mfundo za m’Baibulo tidzakhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Chikhulupirirochi chingakhale ngati nangula yemwe amathandiza kuti boti lisatengedwe ndi mphepo yamkuntho. w20.07 9 ¶6-7

Lachinayi, November 3

Anatilamula kuti tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira.​—Mac. 10:42.

Yesu amaona kuti zimene timachita pothandiza abale ake odzozedwa, tikuchitira iyeyo. (Mat. 25:34-40) Njira yofunika kwambiri imene tingathandizire odzozedwa ndi kugwira nawo mwakhama ntchito yophunzitsa anthu yomwe Yesu analamula otsatira ake kuti aziigwira. (Mat. 28:19, 20) Abale a Khristu angakwanitse kugwira ntchito yolalikira padziko lonse pokhapokha ngati akuthandizidwa ndi a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Ngati ndinu a nkhosa zina, nthawi iliyonse imene mumagwira ntchitoyi mumasonyeza kuti mumakonda odzozedwa komanso Yesu. Timagwirizananso ndi Yehova ndi Yesu tikamapereka ndalama zathu kuti zithandize pa ntchito imene akutsogolera. (Luka 16:9) Tingapereke ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Ndalama zimenezi zimathandiza polalikira m’madera akutali, pomanga ndi kukonza malo olambirira komanso pothandiza anthu amene akumana ndi ngozi zadzidzidzi. Tikhozanso kupereka ndalama zothandiza pampingo wathu ndiponso kuthandiza abale athu amene akuvutika.​—Miy. 19:17. w20.04 24 ¶12-13

Lachisanu, November 4

Iyo sidzaganizira Mulungu wa makolo ake. . . . Ndipo idzapereka ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.—Dan. 11:37, 38.

Pokwaniritsa ulosiwu, mfumu ya kumpoto ‘sinaganizire Mulungu wa makolo ake.’ Kodi inachita bwanji zimenezi? Boma la Soviet Union linayesa kulanda mphamvu zimene zipembedzo zinali nazo ndi cholinga chofuna kuzithetsa. Kuti likwanitse kuchita zimenezi, mu 1918 bomali linakhazikitsa lamulo lomwe linachititsa kuti masukulu aziphunzitsa zoti kulibe Mulungu. Nanga kodi mfumu ya kumpoto inapereka bwanji “ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri”? Boma la Soviet Union linawononga ndalama zambiri polimbitsa chitetezo chake pa nkhondo komanso popanga zida zambiri zanyukiliya. Kenako mfumuyi komanso mfumu ya kum’mwera anali ndi zida zamphamvu kwambiri zomwe zikanatha kupha anthu mabiliyoni. Mfumu ya kumpoto inathandiza mfumu ya kum’mwera poika “chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko,” bungwe la United Nations.​—Dan. 11:31. w20.05 6-7 ¶16-17

Loweruka, November 5

M’bale wakoyu . . . anali wotayika koma tsopano wapezeka.​—Luka 15:32.

Kodi ndi ndani angagwire nawo ntchito yofufuza anthu amene anasiya kusonkhana? Aliyense angagwire nawo ntchitoyi, kaya ndi akulu, apainiya, achibale a munthuyo komanso ofalitsa onse mumpingo. Ndiye kodi muli ndi mnzanu kapena wachibale amene anasiya kusonkhana? Kodi mungachite chiyani ngati mwakumana ndi munthu amene anasiya kusonkhana pamene mukulalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo opezeka anthu ambiri? Mungamufotokozere kuti ngati angakonde kuti akulu a mumpingo wanu amuyendere, mukhoza kukawapatsa nambala yafoni kapena adiresi yake. Mkulu wina dzina lake Thomas, anati: “Choyamba ndimafunsa abale ndi alongo osiyanasiyana ngati akudziwa kumene anthuwo akukhala panopa. Apo ayi ndimafunsa ofalitsa ngati akukumbukira anthu ena amene sakufikanso pamisonkhano. Ndiyeno ndikayendera abale ndi alongo amene anasiya kusonkhanawo, ndimafunsa za ana komanso achibale awo ena. Ena mwa abale ndi alongowa ankabwera ndi ana komanso achibale awo ena kumisonkhano, omwe mwinanso anali ofalitsa. Amenewanso tingawathandize kuti abwerere kwa Yehova.” w20.06 24 ¶1; 25 ¶6-7

Lamlungu, November 6

Ndidzakumbukira zochita za Ya, ndithu ndidzakumbukira ntchito yanu yodabwitsa yakale.​—Sal. 77:11.

Pa zamoyo zonse zomwe zili padzikoli, ndi anthu okha omwe amatha kuphunzira zinthu pokumbukira zomwe zinawachitikira m’mbuyo. Zimenezi zimatithandiza kukhazikitsa mfundo zoti tiziyendera komanso kusintha mmene timaonera zinthu. (1 Akor. 6:9-11; Akol. 3:9, 10) Timatha kuphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera. (Aheb. 5:14) Timathanso kuphunzira kukonda ndi kusonyeza chifundo anthu ena. Komanso timaphunzira kuchita zinthu mwachilungamo potsanzira Yehova. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso yokumbukira zinthu, ndi kuyesetsa kukumbukira maulendo onse omwe Yehova wakhala akutithandiza. Zimenezi zingatilimbitse mtima kuti ngakhale m’tsogolo, Yehova adzakhalabe nafe. (Sal. 77: 12; 78:4, 7) Njira inanso, ndi kukumbukira zinthu zabwino zomwe anthu ena anatichitira komanso kuwayamikira chifukwa cha zomwe amachita. Ochita kafukufuku anapeza kuti anthu amene amayamikira ena amakhala osangalala. w20.05 23 ¶12-13

Lolemba, November 7

Uziopa dzina laulemerero ndi lochititsa manthali, dzina lakuti Yehova.​—Deut. 28:58.

Taganizirani mmene Mose anamvera ataona masomphenya osonyeza ulemerero wa Mulungu. Pa nthawiyi iye anabisala kuphanga lathanthwe. N’kutheka kuti palibe aliyense amene anaonapo zinthu zoopsa ngati zimenezi. Mose anamva mawu akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.” (Eks. 33:17-23; 34:5-7) N’zosakayikitsa kuti mawuwa analankhulidwa ndi mngelo. N’kutheka kuti nthawi zonse Mose akangotchula za dzina la Yehova ankakumbukira zomwe zinachitika pa nthawiyi. Tikamaganizira za dzina la Yehova, tingachitenso bwino kuganizira makhalidwe omwe ali nawo. Tiyenera kuganizira za makhalidwe ake monga mphamvu, nzeru, chilungamo komanso chikondi. Tikamaganizira za makhalidwewa komanso ena, zingatithandize kuti tizimulemekeza kwambiri.​—Sal. 77:11-15. w20.06 8-9 ¶3-4

Lachiwiri, November 8

Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo.​—2 Tim. 3:14.

Yesu ananena kuti anthu adzadziwa ophunzira ake chifukwa amakondana. (Yoh.13:34, 35) Koma pali zinanso zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Chikhulupiriro chathu sichiyenera kungodalira chikondi chomwe timaona pakati pa anthu a Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Tayerekezerani kuti wokhulupirira mnzanu, mkulu kapena mpainiya wachita tchimo lalikulu. Mwinanso m’bale kapena mlongo wina wakukhumudwitsani. Kapenanso wina wayamba mpatuko ndipo akunena kuti zimene timakhulupirira si zoona. Ngati zimenezi zitachitika, kodi mungakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? Pamenepa mfundo ndi yakuti: Ngati mumakhulupirira Yehova chifukwa cha zochita za anthu ena osati chifukwa choti muli naye pa ubwenzi wolimba, chikhulupiriro chanu sichingakhale cholimba. N’zoona kuti mmene mumaonera Yehova komanso anthu ake zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Koma n’zofunikanso kwambiri kumaphunzira Baibulo mwakhama, kumvetsa zimene mukuphunzirazo komanso kufufuza mfundo zina. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzitsimikizira kuti zomwe mukuphunzira zokhudza Yehova ndi zoona.​—Aroma 12:2. w20.07 8 ¶2-3

Lachitatu, November 9

Muthandize ofookawo.​—Mac. 20:35.

Pali zitsanzo zambiri zomwe zimasonyeza kuti angelo amatithandiza tikamafufuza anthu amene akufuna kubwerera kwa Yehova. (Chiv. 14:6) Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Ecuador dzina lake Silvio, ankapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kubwerera kwa iye. Asanamalize kupemphera, akulu awiri anafika pakhomo pake. Akuluwo anamufotokozera zimene angachite ndipo anali ofunitsitsa kumuthandiza. Tikamathandiza anthu amene anafooka, timakhala osangalala kwambiri. Mpainiya wina dzina lake Salvador, amayesetsa kuthandiza anthu amene anafooka. Iye anati: “Ndikamaganizira za ofalitsa ena ofooka amene anabwerera kwa Yehova, ndimasangalala kwambiri moti nthawi zina ndimagwetsa misozi. Zimandisangalatsa kuona kuti Yehova wapulumutsa nkhosa yake kuchokera kudziko la Satanali ndipo ndinali ndi mwayi wothandiza nawo kuti zimenezi zitheke.” Ngati munasiya kupezeka pamisonkhano, muyenera kudziwa kuti Yehova amakukondanibe. Yehova akuyembekezera kuti mubwerere kwa iye, ndipo adzakulandirani ndi manja awiri. w20.06 29 ¶16-18

Lachinayi, November 10

Maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.​—Yes. 30:20.

Yehova yemwe ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ amatipatsa zitsanzo zotiphunzitsa kudzera m’Mawu ake. (Yes. 30:21) Timaphunzira zambiri tikamaganizira nkhani za anthu ena otchulidwa m’Baibulo omwe anasonyeza makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo. Timaphunziranso zambiri pa zimene zinachitikira anthu ena amene sanasonyeze makhalidwewa. (Sal. 37:37; 1 Akor. 10:11) Taganizirani zimene zinachitikira Mfumu Sauli. Ali mnyamata, anali wodzichepetsa. Iye ankadziwa malire ake moti nthawi ina anakayikira kuti sakanakwanitsa kukhala ndi udindo waukulu. (1 Sam. 9:21; 10:20-22) Koma patapita nthawi, Sauli anayamba kudzikweza ndipo anachita zinthu zimene sankayenera kuchita. Anayamba kusonyeza khalidweli atangokhala mfumu. Pa nthawi ina, analephera kudikira moleza mtima kuti mneneri Samueli afike ndipo anapereka nsembe ngakhale kuti umenewu sunali udindo wake. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova asiye kumukonda ndipo pamapeto pake ufumu wake unatha. (1 Sam. 13:8-14) Chitsanzochi chikutiphunzitsa kuti tiyenera kupewa kuchita zinthu modzikweza. w20.08 10 ¶10-11

Lachisanu, November 11

Muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye.​—1 Ates. 5:12.

Ndi zoona kuti kudzera mwa Khristu, Yehova anapereka “mphatso za amuna” mumpingo. (Aef. 4:8) Mphatso za amuna zimenezi zikuphatikizapo abale a m’Bungwe Lolamulira, othandizira abale a m’Bungwe Lolamulira, abale a m’Makomiti a Nthambi, oyang’anira madera, abale amene amaphunzitsa sukulu zophunzitsa Baibulo, akulu mumpingo komanso atumiki othandiza. Abale onsewa amasankhidwa ndi mzimu woyera kuti azisamalira nkhosa za Yehova zomwe ndi zamtengo wapatali komanso kulimbikitsa abale ndi alongo mumpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Abale amasankhidwa ndi mzimu woyera kuti azisamalira maudindo osiyanasiyana mumpingo. Ziwalo zosiyanasiyana zathupi monga manja ndi mapazi, zimagwira ntchito kuti zithandize thupi lonse. Mofanana ndi zimenezi, abale amene amasankhidwa ndi mzimu woyera amagwira ntchito mwakhama kuti athandize mpingo wonse. Iwo samachita zimenezi kuti anthu ena aziwapatsa ulemu. M’malomwake, cholinga chawo chimakhala kulimbikitsa abale ndi alongo awo. (1 Ates. 2:6-8) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha abale amenewa, omwe amaganizira kwambiri zofuna za ena m’malo mwa zofuna zawo. w20.08 21 ¶5-6

Loweruka, November 12

Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga.​—Mat. 28:19.

Timadzipereka kugwira ntchito yolalakira n’cholinga choti tithandize anthu “onyukanyuka ndi otayika,” amene amafunitsitsa kuphunzira choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu. (Mat. 9:36) Yehova amafuna kuti anthu kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola (1 Tim. 2:4) Timafunitsitsa kugwira ntchito yolalikira chifukwa tikudziwa kuti idzathandiza anthu kuti adzapulumuke. (Aroma 10:13-15; 1 Tim. 4:16) Timafunikanso kukhala ndi zipangizo zoyenerera zogwiritsa ntchito polalikira komanso kudziwa mmene tingazigwiritsire ntchito. Yesu anapereka malangizo omveka bwino kwa ophunzira ake a mmene angagwirire ntchito yolalikira. Anawauza zomwe ankafunika kutenga, komwe ankayenera kukalalikira komanso zoti akanene. (Mat. 10:5-7; Luka 10:1-11) Masiku ano, gulu la Yehova latipatsa Zinthu Zophunzitsira zimene zimatithandiza pogwira ntchito yolalikira. Limatiphunzitsanso mmene tingazigwiritsire ntchito. Maphunziro amenewa amatithandiza kuti tizigwira ntchito yolalikira molimba mtima komanso mwaluso.​—2 Tim. 2:15. w20.09 4 ¶6-7, 10

Lamlungu, November 13

Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.​—3 Yoh. 4.

Tangoganizani mmene mtumwi Yohane anasangalalira pamene anamva zoti anthu amene anawathandiza kuphunzira choonadi akupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika. Akhristuwa ankakumana ndi mavuto ambiri ndipo Yohane ankayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chawo ndipo ankawaona ngati ana ake. Mofanana ndi Yohane, ifenso timasangalala tikaona ana athu kapena anthu amene timaphunzira nawo Baibulo akudzipereka kwa Yehova n’kumapitiriza kumutumikira. (3 Yoh. 3) M’chaka cha 98 C.E., mzimu wa Yehova unamuthandiza kulemba makalata atatu. Cholinga cha makalatawa chinali kulimbikitsa Akhristu okhulupirika kuti apitirize kukhulupirira Yesu komanso asasiye kuyenda m’choonadi. Yohane ankada nkhawa kwambiri ndi aphunzitsi onyenga omwe ankasokoneza mipingo. (1 Yoh. 2:18, 19, 26) Anthu ampatukowa ankanena kuti amadziwa Mulungu koma sankatsatira malamulo ake. w20.07 20 ¶1-3

Lolemba, November 14

Khulupirirani Mulungu, khulupiriraninso ine.​—Yoh. 14:1.

Timakhulupirira kwambiri uthenga umene timalalikira, choncho timafunitsitsa kuuzako anthu ena mmene tingathere. Timakhulupiriranso kuti malonjezo amene amapezeka m’Baibulo adzakwaniritsidwa. (Sal. 119:42; Yes. 40:8) Taonanso maulosi ambiri a m’Baibulo akukwaniritsidwa masiku ano. Komanso taona anthu akusintha moyo wawo chifukwa choti ayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zimatithandiza kutsimikizira kuti uthenga wabwino ndi ofunika kwa munthu aliyense. Timakhulupiriranso Yehova yemwe ndi mwini wake wa uthenga umene timalalikirawu komanso timakhulupirira Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kaya tikukumana ndi zotani, Yehova adzakhalabe pothawira pathu ndi mphamvu yathu. (Sal. 46:1-3) Komanso sitikukayikira kuti Yesu akupitirizabe kutsogolera ntchito yolalikira, pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Yehova anamupatsa. (Mat. 28:18-20) Chikhulupiriro chimatithandiza kuti tisamakaikire kuti Yehova adzadalitsa khama lathu. w20.09 12 ¶15-17

Lachiwiri, November 15

Iyetu wandichitira zinthu zabwino. . . . Mayiyu wachita zimene angathe.​—Maliko 14:6, 8.

Nthawi zina, alongo amafuna kuti munthu wina awateteze akamakumana ndi mavuto ena ake. (Yes. 1:17) Mwachitsanzo mlongo amene ndi wamasiye kapena amene banja lake linatha, angafune munthu wina kuti amuthandize kuchita zinthu zina zimene mwamuna wake ankachita. Mlongo wina wachikulire angafune kuti munthu wina amuthandize kulankhulana ndi madokotala. Komanso mlongo yemwe ndi mpainiya, amene amagwira ntchito zina m’gulu la Yehova, angafunike munthu womuteteza anthu ena akamamunena kuti salowalowa muutumiki ngati mmene apainiya ena amachitira. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Yesu ankalankhulapo mwamsanga pofuna kuteteza alongo ake pamene anthu ena sankawamvetsa. Mwachitsanzo anateteza Mariya pamene Marita ankamuimba mlandu. (Luka 10:38-42) Anatetezanso Mariya ulendo wina pamene anthu ena ankaona kuti wachita zinthu mosaganiza bwino. (Maliko 14:3-9) Yesu ankaona kuti Mariya anachita zimenezi ndi cholinga chabwino ndipo anamuyamikira. Iye analoseranso kuti zabwino zimene mayiyu anachita, zidzadziwika “kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe m’dziko lonse.” w20.09 24 ¶15-16

Lachitatu, November 16

Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.​—1 Pet. 5:2.

M’busa wabwino ankadziwa kuti nkhosa ikhoza kusochera. Choncho nkhosa ikasiyana ndi zinzake, sankaichitira nkhanza. Tiyeni tione chitsanzo chimene Yehova anasonyeza pothandiza atumiki ake ena omwe kwa kanthawi anasiya kuchita zimene iye anawauza. Nthawi ina mneneri Yona sanamvere zimene Yehova anamuuza kuti apite ku Nineve. Ngakhale zinali choncho, Yehova sanamusiye. Monga m’busa wabwino, anamuthandiza kuti apezenso mphamvu zimene ankafunikira kuti akwaniritse utumiki wake. (Yona 2:7; 3:1, 2) Kenako iye anagwiritsa ntchito chomera cha mtundu wamphonda pofuna kuthandiza Yona kumvetsa kuti moyo wa munthu aliyense ndi wofunika kwambiri. (Yona 4:10, 11) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani? Akulu sayenera kutaya mtima msanga akamathandiza anthu amene afooka. M’malomwake ayenera kumvetsa chimene chinachititsa kuti anthuwo afooke. Ndiyeno munthuyo akabwerera kwa Yehova, akulu amapitiriza kumusonyeza chikondi komanso kuti amamuganizira. w20.06 20-21 ¶10-12

Lachinayi, November 17

Adzathandizidwa ndi thandizo lochepa.​—Dan. 11:34.

Ulamuliro wa Soviet Union utatha mu 1991, anthu a Mulungu omwe ankakhala m’madera olamuliridwa ndi bomali anakhala pa ufulu kwa kanthawi. Danieli anatchula ufulu umenewu kuti “thandizo lochepa.” Zimenezi zinathandiza kuti azilalikira mwaufulu ndipo pasanapite nthawi chiwerengero cha ofalitsa m’mayiko amenewa chinawonjezereka kwambiri. Koma patadutsa zaka, dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo anakhala mfumu ya kumpoto. Kuti ulamuliro ukhale mfumu ya kumpoto kapena mfumu ya kum’mwera uyenera kuchita zinthu zitatu izi: (1) kulamulira komanso kuzunza anthu a Mulungu, (2) kuchita zinthu zosonyeza kuti amadana ndi Yehova komanso anthu ake, ndiponso (3) kulimbirana ulamuliro ndi mfumu inayo. Tinganene kuti masiku ano mfumu ya kumpoto ndi dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo chifukwa iwo akuukira anthu a Mulungu poletsa ntchito yolalikira komanso kuzunza abale ndi alongo ambiri omwe amakhala m’mayikowo. Zimene akuchita zikusonyeza kuti amadana ndi Yehova komanso anthu ake. Komanso iwo akulimbana ndi mfumu ya kum’mwera, yomwe ndi ulamuliro wa Britain ndi America. w20.05 12-13 ¶3-4

Lachisanu, November 18

Nthawi zonse uzisamala ndi . . . zimene umaphunzitsa.​—1 Tim. 4:16.

Popeza ntchito yophunzitsa ndi imene imathandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, tiyenera kuchita khama kuti tiziphunzitsa bwino. Timaphunzira Baibulo ndi anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse ndipo timakonda kwambiri zimene timaphunzitsa kuchokera m’Mawu a Mulungu. Choncho mwina tikhoza kumalankhula kwambiri tikamaphunzitsa anthu Baibulo. Komabe, kaya tikuchititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, Phunziro la Baibulo la Mpingo kapena phunziro la Baibulo lapanyumba, tizikumbukira kuti sitiyenera kumalankhula kwambiri. Kuti tizigwiritsa ntchito Baibulo pophunzitsa, tiyenera kukhala odziletsa ndipo tiziyesetsa kupewa kufotokoza zinthu zonse zimene tikudziwa zokhudza lemba kapena nkhani inayake. (Yoh. 16:12) Yerekezerani zimene munkadziwa zokhudza Baibulo pa nthawi imene munkabatizidwa ndi zimene mukudziwa panopa. N’kutheka kuti pa nthawiyo munkangodziwa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. (Aheb. 6:1) Panopa mukudziwa zochuluka chifukwa mwakhala mukuphunzira Baibulo kwa zaka zambiri. Choncho tizipewa kuphunzitsa wophunzira wathu zinthu zonse zimene tikudziwa nthawi imodzi. w20.10 14-15 ¶2-4

Loweruka, November 19

Kodi iyeyu si mmisiri wamatabwa, mwana wa Mariya?​—Maliko 6:3.

Yehova anasankhira Yesu makolo abwino kwambiri. (Mat. 1:18-23; Luka 1:26-38) Mawu a Mariya ochokera pansi pamtima amene amapezeka m’Baibulo, amasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehova komanso Mawu ake. (Luka 1:46-55) Komanso zimene Yosefe ankachita pomvera malangizo a Yehova, zimasonyeza kuti ankakonda Mulungu ndipo ankafunitsitsa kumusangalatsa. (Mat. 1:24) Kumbukirani kuti Yehova sanamusankhire Yesu makolo olemera. Nsembe imene Yosefe ndi Mariya anapereka Yesu atabadwa imasonyeza kuti anali osauka. (Luka 2:24) Banjali liyenera kuti linalibe ndalama komanso zinthu zambiri makamaka chifukwa chakuti linali banja lalikulu, lokhala ndi ana 7 kapena kuposa. (Mat. 13:55, 56) Yehova ankateteza Yesu pa zinthu zina koma sanamuteteze pa mavuto onse amene anakumana nawo. (Mat. 2:13-15) Mwachitsanzo, Yesu anali ndi achibale ake ena omwe poyamba sankakhulupirira kuti iye anali Mesiya. (Maliko 3:21; Yoh. 7:5) Zikuonekanso kuti Yosefe anamwalira Yesu adakali wamng’ono ndipo zimenezi zinali zopweteka kwambiri kwa iye. w20.10 26-27 ¶4-6

Lamlungu, November 20

Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.​—Aheb. 13:5.

Kodi nthawi zina mumamva kuti muli nokhanokha ndipo palibe amene angakuthandizeni pa mavuto anu? Ambiri amamvanso choncho, kuphatikizapo atumiki okhulupirika a Yehova. (1 Maf. 19:14) Ngati inunso mutayamba kumva choncho, muzikumbukira lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Choncho tinganene molimba mtima kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.” (Aheb. 13:5, 6) Mtumwi Paulo analembera mawu amenewa okhulupirira anzake a ku Yudeya cha m’ma 61 C.E. Mawu akewa akutikumbutsa zimene wolemba masalimo ananena pa Salimo 118:5-7. Mofanana ndi wolemba masalimoyu, Paulo ankadziwa kuti Yehova angamuthandize chifukwa anamuthandizapo kambirimbiri m’mbuyomu. Mwachitsanzo, zaka zoposa ziwiri asanalembe kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo anapulumuka chimphepo choopsa pamene ankayenda panyanja. (Mac. 27:4, 15, 20) Pa ulendo wonsewu komanso kwa zaka zambiri asananyamuke ulendowu, Yehova anathandiza Paulo m’njira zosiyanasiyana. w20.11 12 ¶1-2

Lolemba, November 21

Usanene kuti: “N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?”​—Mlal. 7:10.

N’chifukwa chiyani si nzeru kumangoganiza kuti kale zinthu zinali bwino? Kulakalaka zinthu zakale kungatichititse kuti tizingokumbukira zinthu zabwino zokhazokha zimene zinachitika pa moyo wathu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira Aisiraeli. Atangochoka ku Iguputo, mwamsanga anaiwala mavuto amene ankakumana nawo ali m’dzikoli. M’malomwake ankangoganizira za chakudya chabwino chimene ankadya. Iwo anati: “Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinali kudya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!” (Num. 11:5) Koma kodi n’zoona kuti zakudyazi zinali zaulere? Ayi si zinali zaulere chifukwa pa nthawi imene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo ankaponderezedwa kwambiri. (Eks. 1:13, 14; 3:6-9) Koma pambuyo pake iwo anaiwala mavuto onse amene ankakumana nawo n’kuyamba kulakalaka zinthu zakale. Iwo anasankha kumangoganizira zimene ankasangalala nazo m’mbuyomo, m’malo moganizira zinthu zabwino zimene Yehova anali atawachitira. Yehova sanasangalale ndi zimenezi.​—Num. 11:10. w20.11 25 ¶5-6

Lachiwiri, November 22

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.​—Sal. 34:18.

Moyo wathu ndi waufupi komanso “wodzadza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Zimenezi nthawi zina zimachititsa kuti tikhale osweka mtima. Atumiki ena a Yehova m’mbuyomu zimenezi zinawachitikirapo, moti ena anafika poona kuti bola angofa. (1 Maf. 19:2-4; Yobu 3:1-3, 11; 7:15, 16) Koma nthawi zonse Yehova amene ankamukhulupirira ankawalimbikitsa komanso kuwapatsa mphamvu. Nkhani za anthu amenewa zinalembedwa kuti zizitilimbikitsa komanso kutilangiza. (Aroma 15:4) Taganizirani za Yosefe mwana wa Yakobo. M’kanthawi kochepa moyo wake unasintha kwambiri, kuchoka pa mwana wokondedwa ndi bambo ake n’kukhala kapolo wa Mwiguputo yemwe sankalambira Yehova. (Gen. 37:3, 4, 21-28; 39:1) Kenako mkazi wa Potifara ananamizira Yosefe kuti ankafuna kumugwiririra. Potifara sanafufuze kuti adziwe zoona, m’malomwake anangolamula kuti Yosefe amangidwe unyolo ndipo amuike m’ndende. (Gen. 39:14-20; Sal. 105:17, 18). Kunena zoona, izi zinachititsa kuti Yosefe akhale wosweka mtima. w20.12 16-17 ¶1-4

Lachitatu, November 23

Dzina lanu liyeretsedwe.​—Mat. 6:9.

Yesu anasonyeza kuti kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu ndi mfundo yofunika kuikumbukira tikamapemphera. Koma kodi ankatanthauza chiyani? Mawu akuti kuyeretsa palembali amatanthauza kuchititsa chinthu kukhala chopatulika. Koma mwina ena angafunse kuti, ‘Kodi dzina la Yehova si loyera kale, ndiye lingafunikenso kuliyeretsa?’ Kuti tiyankhe bwino funsoli, tiyenera kuganizira zimene dzina limatanthauza. Dzina si mawu amene timangogwiritsa ntchito potchulira munthu kapena chinthu chinachake basi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.” (Miy. 22:1; Mlal. 7:1) N’chifukwa chiyani dzina lili lofunika kwambiri chonchi? Chifukwa dzina lingatanthauzenso mbiri ya munthu komanso zimene ena amadziwa zokhudza munthuyo. Choncho kalembedwe kapena katchulidwe ka dzina si zofunika kwenikweni. Chofunika ndi zomwe anthu amaganiza akamva dzinalo. Anthu akamanenera Yehova zinthu zabodza, amakhala akuipitsa mbiri yake. Akamachita zimenezi amakhalanso kuti akudetsa dzina lake. w20.06 3 ¶5-7

Lachinayi, November 24

Moyo wanga wasokonezeka kwambiri. Kodi inu Yehova, mudzadikira kufikira liti?​—Sal. 6:3.

Nthawi zina anthufe tingamade nkhawa mpaka kufika posiya kuganiza bwino. Mwachitsanzo, tikhoza kumada nkhawa kuti sitizipeza ndalama zokwanira zogulira zinthu zofunika pa moyo wathu, tidwala mpaka kujomba kuntchito, komanso kuti mwina ntchito ikhoza kutithera. Tikhozanso kumaona ngati tidzalephera kukhala okhulupirika tikadzayesedwa kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Posachedwapa Satana adzachititsa anthu amene iyeyo amawatsogolera kuti aukire atumiki a Mulungu. Choncho tikhoza kumada nkhawa n’kumaganiza kuti ‘kodi tidzatani zimenezi zikadzachitika?’ Ndiye mwina mungamadzifunse kuti: ‘Kodi n’kulakwa kukhala ndi nkhawa pa nkhani zimenezi?’ Tikudziwa kuti Yesu anauza otsatira ake kuti: “Lekani kudera nkhawa.” (Mat. 6:25) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ankayembekezera kuti sitizida nkhawa ndi chilichonse? Ayi. Ndipotu atumiki ena a Yehova okhulupirika m’mbuyomu anadapo nkhawa ndi zinthu zina. Koma si kuti Yehova anasiya kuwakonda. (1 Maf. 19:4) Apa Yesu ankafuna kutithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri kuti tipeza bwanji zinthu zimene tikufuna, mpaka kufika polephera kuona kuti utumiki wathu kwa Mulungu ndi wofunika. w21.01 3 ¶4-5

Lachisanu, November 25

Mutu wa mkazi ndi mwamuna.​—1 Akor. 11:3.

Yehova ndi Yesu amafuna kuti mwamuna azigwiritsa ntchito bwino udindo wake. (1 Pet. 3:7) Popeza kuti Yehova ndi mutu wa banja lake lakumwamba komanso padziko lapansi, iye ali ndi mphamvu zopanga malamulo oti ana ake azitsatira komanso kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa. (Yes. 33:22) Nayenso Yesu yemwe ndi mutu wampingo, ali ndi mphamvu zopanga malamulo komanso kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa. (Agal. 6:2; Akol. 1:18-20) Mofanana ndi Yehova komanso Yesu, mwamuna ali ndi udindo wosankha zochita zokhudza banja lake. (Aroma 7:2; Aef. 6:4) Komabe udindo wake uli ndi malire. Mwachitsanzo, malamulo amene amapanga ayenera kukhala ogwirizana ndi mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu. (Miy. 3:5, 6) Komanso mwamuna alibe udindo wopangira malamulo anthu ena omwe si a m’banja lake. (Aroma 14:4). Ndipo ana ake akakula n’kuchoka pakhomo, anawo amapitirizabe kumulemekeza koma iye sapitiriza kuwatsogolera monga mutu wawo.​—Mat. 19:5. w21.02 2-3 ¶3-5

Loweruka, November 26

Muzisamalira anthu amene ndi udindo [wanu] kuwasamalira.​—1 Tim. 5:8.

Njira imodzi imene mwamuna yemwe ndi mutu wa banja angasonyezere kuti amakonda anthu a m’banja lake, ndi kuwapezera zinthu zofunika pa moyo. Koma iye ayenera kukumbukira kuti chofunika kwambiri ndi kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Mat. 5:3) Pamene Yesu anali pamtengo wozunzikirapo ankaganizirabe anthu a m’banja lake. Ngakhale kuti anali mu ululu waukulu, anapempha Yohane kuti azisamalira mayi ake. (Yoh. 19:26, 27) M’bale yemwe ndi mutu wa banja, amakhala ndi maudindo ambiri. Ngati amagwira ntchito yolembedwa, iye ayenera kumagwira ntchitoyo mwakhama n’cholinga choti khalidwe lake lizilemekezetsa dzina la Yehova. (Aef. 6:5, 6; Tito 2:9, 10) Iye angakhalenso ndi maudindo ena mumpingo, monga kulimbikitsa abale ndi alongo komanso kutsogolera pa ntchito yolalikira. Kuwonjezera pamenepo, amafunikanso kuti nthawi zonse aziphunzira Baibulo ndi mkazi wake komanso ana ake. Anthu a m’banja lake amamuyamikira chifukwa chowathandiza kuti akhale a thanzi, azisangalala komanso azipitirizabe kutumikira Yehova.​—Aef. 5:28, 29; 6:4. w21.01 12 ¶15, 17

Lamlungu, November 27

[Mkazi wabwino] amayang’anira zochitika za pabanja pake.​—Miy. 31:27.

Baibulo limafotokoza zimene mkazi wabwino angachite. Mwachitsanzo, iye angathe kuyang’anira ntchito zonse zapakhomo, kugula kapena kugulitsa malo komanso kuchita bizinezi. (Miy. 31:15, 16, 18) Iye si kapolo amene alibe ufulu wofotokoza maganizo ake. M’malomwake, mwamuna wake amamudalira ndipo amamumvetsera akamafotokoza maganizo akewo. (Miy. 31:11, 26) Mwamuna akamalemekeza mkazi wake mwa njira imeneyi, zimachititsa kuti mkaziyo azimugonjera mosangalala. Ngakhale kuti Yesu anachita zinthu zazikulu, iye samaona kuti angaoneke wotsika akamagonjera Yehova ngati mutu wake. (1 Akor. 15:28; Afil. 2:5, 6) Mofanana ndi zimenezi, mkazi wabwino amene amatengera chitsanzo cha Yesu, samaona kuti aoneka wotsika akamagonjera mwamuna wake. N’zoona kuti amathandiza mwamuna wake chifukwa choti amamukonda, koma chifukwa chachikulu chimene amachitira zimenezi n’chakuti amakonda komanso kulemekeza Yehova. Choncho Mkazi wa Chikhristu amene amagonjera mwamuna wake sangalole kuchita zimene mwamuna wake wamupempha, ngati zinthuzo zikusemphana ndi malamulo kapena mfundo za m’Baibulo. w21.02 11 ¶14-15; 12 ¶19

Lolemba, November 28

Chisautso chimabala chipiriro.—Aroma 5:3.

Kukonda Mulungu kwathandiza atumiki a Yehova kuti azipirira akamazunzidwa. Mwachitsanzo, atumwi atalamulidwa ndi khoti lalikulu la Ayuda kuti asiye kulalikira, kukonda Mulungu kunawathandiza kuti ‘amvere Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’ (Mac. 5:29; 1 Yoh. 5:3) Chikondi ngati chimenechi ndi chomwe chikuthandizanso abale athu masiku ano kukhalabe okhulupirika akamazunzidwa ndi maboma amphamvu komanso ankhanza. Choncho, m’malo mofooka anthu a m’dzikoli akamadana nafe, timasangalala. (Mac. 5:41; Aroma 5:4, 5) Chimodzi mwa zinthu zovuta kwambiri kupirira ndi kutsutsidwa ndi achibale athu. Pamene tayamba kusonyeza chidwi chofuna kuphunzira za Yehova, achibale athu angaganize kuti tasocheretsedwa. Ndipo ena akhoza kumaona kuti sitikuganiza bwino. (Yerekezerani ndi Maliko 3:21.) Mwinanso angamatichitire nkhanza. Komatu zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Yesu ananena kuti: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.”​—Mat. 10:36. w21.03 21 ¶6-7

Lachiwiri, November 29

Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.—Yak. 1:19.

Mukapita ndi wofalitsa kuphunziro lake la Baibulo muzimvetsera mwatcheru mphunzitsiyo akamakambirana ndi wophunzirayo. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa nthawi yoyenera kulankhula. Komabe muyenera kuganizira kaye musanayambe kulankhula. Mwachitsanzo, simuyenera kulankhula kwambiri, kumudula mawu mphunzitsiyo kapena kuyambitsa nkhani ina. Koma mukhoza kumveketsa mfundo imene akukambiranayo popereka ndemanga yachidule, fanizo kapena funso. Nthawi zina mungaone kuti palibe zambiri zomwe mungalankhulepo. Koma ngati mungamuyamikire wophunzirayo komanso kumusonyeza kuti mukuchita naye chidwi, mungamuthandize kwambiri kuti apite patsogolo. Ngati zingakhale zothandiza kwa wophunzirayo, mungamufotokozere mwachidule mmene munaphunzirira choonadi, zimene zinakuthandizani mutakumana ndi mavuto enaake kapenanso mmene Yehova wakuthandizirani pa moyo wanu. (Sal. 78:4, 7) N’kutheka kuti zimene mungafotokoze zingamuthandize kwambiri wophunzirayo. Zingalimbitse chikhulupiriro chake kapena kumulimbikitsa kuti apitirize kuphunzira mpaka kufika pobatizidwa. w21.03 10 ¶9-10

Lachitatu, November 30

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.—Mat. 28:19.

Kodi ndi ndani amene ayenera kutamandidwa zinthu zikamatiyendera bwino pa ntchito yathu yolalikira? Paulo anapereka yankho la funsoli mukalata yake yopita ku mpingo wa Akorinto. Iye anati: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa. Chotero wobzala kapena wothirira sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.” (1 Akor. 3:6, 7) Mofanana ndi Paulo, nafenso tiyenera kutamanda Yehova zinthu zikamatiyendera bwino pa ntchito yathu yolalikira. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mwayi umene tili nawo ‘wogwira ntchito limodzi’ ndi Yehova, Khristu komanso angelo? (2 Akor. 6:1) Tingachite zimenezi tikamachita khama kuuza ena uthenga wabwino. Sitiyenera kumangodzala mbewu za choonadi koma tiyeneranso kumazithirira. Tikapeza munthu amene wasonyeza chidwi, tiziyesetsa kubwererakonso kapena kukonza zoti munthu wina adzapiteko n’cholinga choti akayambe kuphunzira naye Baibulo. Timasangalala tikaona kuti munthu amene tikuphunzira naye, Yehova akumuthandiza kusintha mmene amaganizira komanso zochita zake. w20.05 30 ¶14, 16-18

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena